Sermons

[16-1] < Chivumbulutso 16:1-21 > Chiyambi cha Miliri ya Mbale zisanu ndi Ziwiri

 

 

< Chivumbulutso 16:1-21 >

Kenako, ndinamvamawu ofuula ochokera m’malo opatulika akuuza angelo 7 aja kuti: “Pitani, kathireni mbale 7 za mkwiyo wa Mulunguzo kudziko lapansi.” Mngelo woyamba anapita n’kukathira mbale yake padziko lapansi. Pamenepo mliriwa zilonda zopweteka ndi zonyekaa unagwa pakati pa anthu amene anali ndi chizindikiro cha chilombo, a amenenso anali kulambira chifaniziro chake. Mngelo wachiwiri anathira mbale yake m’nyanja. Ndipo nyanja inasanduka magazi ngati a munthu wakufa, moti chamoyo chilichonse m’nyanjamo chinafa. Mngelo wachitatu anathira mbale yake pamitsinje ndi pa akasupe amadzi, ndipo zonse zinasanduka magazi. 5 Ndiye ndinamva mngelo wokhala ndi ulamuliro pa madzi akunena kuti:

Inu Amene mulipo ndi amene munalipo,

Inu Wokhulupirika, ndinu wolungama

chifukwa mwapereka zigamulo zimenezi,

pakuti iwo anakhetsa magazi a oyera ndi aneneri.

Ndipo inu mwawapatsa magazi kuti amwe, ndipo n’zowayenereradi.”

7 Kenako ndinamva guwa lansembe likunena kuti: “Inde, Yehova Mulungu, inuWamphamvuyonse, zigamulo zanu n’zoona ndi zolungama.” Mngelo wachinayi anathira mbale yake padzuwa. Ndipo dzuwa linaloledwa kutentha anthu ndi moto. Choncho anthu anapsa ndi kutentha kwakukulu. Koma iwo ananyoza dzina la Mulungu, amene ali ndi ulamulirou pamiliri imeneyi, ndipo sanalape kuti amupatse ulemerero. Mngelo wachisanu anathira mbale yake pampando wachifumu wa chilombo. Pamenepo ufumu wake unachita mdima, ndipo anthu anayamba kudziluma malilime chifukwa cha ululu. Koma iwo ananyoza Mulungu wakumwamba chifukwa cha ululu wawo ndi zilonda zawo, ndipo sanalape ntchito zawo. Mngelo wa 6 anathira mbale yake pamtsinje waukulu wa Firate, ndipo madzi ake anauma, a kuti njira ya mafumu ochokera kotulukira dzuwa ikonzedwe. Kenako ndinaona mauthenga atatu onyansa ouziridwa, ooneka ngati achule, akutuluka m’kamwa mwa chinjoka, m’kamwa mwa chilombo, ndi m’kamwa mwa mneneri wonyenga. Kwenikweni amenewa ndi mauthenga ouziridwah ndi ziwanda ndipo amachita zizindikiro. Mauthengawo akupita kwa mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti awasonkhanitsire pamodzi kunkhondo ya tsiku lalikulum laMulungu Wamphamvuyonse. “Taona! Ndikubwera ngati mbala. Wodala ndiye amene akhalabe maso ndi kukhalabe chivalire malaya ake akunja, kuti asayende wosavala anthu n’kuona maliseche ake.” Ndipo anawasonkhanitsa pamodzi, kumalo amene m’Chiheberi amatchedwa Haramagedo. Ndiyeno mngelo wa 7 anakhuthulira mbale yake pampweya. Atatero, kunamveka mawu ofuula kuchokera m’malo opatulika, kuchokera kumpando wachifumu, akuti: “Zachitika!” Pamenepo kunachitika mphezi, kunamveka mawu, ndipo kunagundamabingu. Kunachitanso chivomezi chachikuluu chimene sichinachitikepo chikhalire anthu padziko lapansi, chivomezi champhamvu kwambiri, chachikulu zedi. Pamenepo mzinda waukulu unagawika zigawo zitatu, ndipo mizinda ya mitundu ya anthu inagwa. Ndiyeno Mulungu anakumbukira Babulo Wamkulu, a kuti amupatse kapu yokhala ndi vinyo wa mkwiyo wake waukulu. Komanso, chilumba chilichonse chinathawa. Ngakhale mapiri sanapezeke. Ndipo matalala aakulu, lililonse lolemera pafupifupi makilogalamu 20, anagwera anthu kuchokera kumwamba. Anthuwo ananyoza Mulungue chifukwa cha mliri wamatalalawo, pakuti mliriwo unali waukulu modabwitsa.”

 

 

Kusanthula

 

Ndime ya 1: Kenako, ndinamvamawu ofuula ochokera m’malo opatulika akuuza angelo 7 aja kuti: “Pitani, kathireni mbale 7 za mkwiyo wa Mulunguzo kudziko lapansi.”

Ndi miliri ya mbale zisanu ndi ziwiri za mkwiyo, Mulungu adzabweretsa mkwiyo Wake pa atumiki a Wosusa Khristu ndi pa anthu Ake amene okhalabe padzikoli lapansi. Zolengedwa zonse ndi anthu adzaonongedwa ndi matalala a mkwiyo wa Mulungu, kuphulika patapita zaka zambiri za kudekha mtima Kwake, ndipo adzadzunzidwa ndi miliri yaikulu imene idzathiridwa pa iwo mnthawi yosala ya zaka zisanu ndi ziwiri za Chisautso Chachikulu. Panthawiyi, dzikoli lidzakhala phulutsa lokha lokha monga mmene lidzaphwanyidwa mziduswa, kuonongedwa mziduswa ziduswa, ndiponso kuonongedwa moiwalidwa.

Chivumbulutso 16 ndi chapitala mmene miliri yam bale zisanu ndi ziwiri ithiridwa. Onse amene, mpaka pa nthawi ino yomaliza, sanadziwa kapena kukhulupilira mu uthenga umene uli ndi umboni wa chipulumutso, umene ukanawalora kuti atengedwe mmtambo ndi Ambuye—umene ndi, uthenga wa madzi ndi Mzimu—onse adzaonongedwa ndi miliriyi.

 

Ndime ya 2: Mngelo woyamba anapita n’kukathira mbale yake padziko lapansi. Pamenepo mliriwa zilonda zopweteka ndi zonyeka unagwa pakati pa anthu amene anali ndi chizindikiro cha chilombo, amenenso anali kulambira chifaniziro chake.

Muliri wa zilonda zopweteka ndiponso zonyeka umene Mulungu adzathira kupyolera mwa mngelo Wake udzatsika pa onse amene analandira chidzindikira cha Chilombo. Muliri wa zilonda ndi nthenda yachikumba yosapola imene idzawoletsa chikumba cha okhuzidwayo, imene kupweteka kwake kudzafalikira kupyola pa chikumba chowolacho. Kudzakhala kwakulu motani kudzunzidwaku, ngati okhuzidwa adzazunzidwa ndi muliriu wa zilonda zopweteka ndiponso zonyeka mpaka imfa yawo? Koma Mulungu sadzathira muliri wa zilonda okha pa onse amene analandira chidzindikiro cha Chilombo, koma Iye adzathiranso miliri ina isanu ndi umodzi pa mitu yawo pambuyo pake. Choncho aliyense ayenera kupeza njira yothawira kuchoka ku miliriyi mu uthenga wa madzi ndi Mzimu, ndi kupewa miliriyi yoopsa pokhulupilira mu uthengau tsopano, panthawi yomweyi.

Ambuye anthu akuti Iye adzathiranso miliri inanso isanu ndi umodzi pa onse amene alambira Chilombo ndi chifaniziro chake. Kodi uchimo umene Mulungu amadana nao kwambiri ndi otani? Uchimou ndi kupanga zifaniziro za china chilichonse kapena za munthu wina aliyense koposa Mulungu, kuzilambira, ndiponso kudzipereka kwa izo. Choncho tiyenera kudziwa moyenera mmene Ambuye Mulungu wathu ndi mmene Yesu Khristu alili, ndi kukhulupilira mwa ndiponso kulambira Yesu Khristu. Kulibe chinthu china ndiponso wina aliyense mdziko lonse, koposa Ambuye Mulungu Iyeyekha, amene angakhalenso Mulungu wathu.

Ngati zoona mfuna kupewa muliri wa zilonda zopweteka ndiponso yoonjezera isanu ndi umodzi, phunzirani za ndipo khulupilirani mu uthenga wa madzi ndi Mzimu wopatsidwa ndi Ambuye. Nambala yosawerengeka ya anthu amene akhala ali kususana ndi Mulungu mu miyoyo yawo ya tsiku ndi tsiku, ndi amene akana kukhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu, onse adzadzunzidwa ndi miliriyi mpaka pomaliza ataonongedwa.

 

Ndime ya 3: Mngelo wachiwiri anathira mbale yake m’nyanja. Ndipo nyanja inasanduka magazi ngati a munthu wakufa, moti chamoyo chilichonse m’nyanjamo chinafa.

Muliri wachiwiri ndi pamene nyanja isanduka magazi ngati ya anthu akufa. Mulungu adzapha zolengedwa zonse zili mnyanja ndi muliriu. Kuchoka pa muliriu wa mbale yachiwiri othiridwa ndi Mulungu, nyanja idzawola ndipo zolengedwa zake zonse sizidzakwanitsanso kukhala mmenemo. Ngakhalenso munthu sadzadyanso zokolora za mnyanja ngati Mulungu wabweretsa muliri wachiwiri, Mulungu adzaonetsa kuti Iye ali moyo, ndi kuti Iye ndi Ambuye pa moyo uliwonse.

Muliriu wachiwiri ndichiweruzo cha Mulungu kuperekedwa ku anthu onse adziko lapansi amene, mmalo molambira Ambuye Mulungu cifukwa cha zolengedwa Zake, mmalo mwake amagwada ku chifaniziro cha Chilombo, mdani wa Mulungu, ndi kukhetsa magazi a oyera. Muliri wachiri ndi oyenereranso kwambiri. Mulungu amationetsa kuti Iye adzachotsa chuma chonse cha khalidwe kuchoka ku onse amene samamuthokoza Mulungu cifukwa zolengedwa zimene zinapangidwa ndi Mulungu.

 

Ndime ya 4-7: Mngelo wachitatu anathira mbale yake pamitsinje ndi pa akasupe amadzi, ndipo zonse zinasanduka magazi. Ndiye ndinamva mngelo wokhala ndi ulamuliro pa madzi akunena kuti: “Inu Amene mulipo ndi amene munalipo, Inu Wokhulupirika, ndinu wolungama chifukwa mwapereka zigamulo zimenezi, pakuti iwo anakhetsa magazi a oyera ndi aneneri. Ndipo inu mwawapatsa magazi kuti amwe, ndipo n’zowayenereradi.” Kenako ndinamva guwa lansembe likunena kuti: “Inde, Yehova Mulungu, inuWamphamvuyonse, zigamulo zanu n’zoona ndi zolungama.”

Muliri wachitatu umene udzasandutsa mitsenje ndi akasupe a madzi mmagazi zoona ndi muliri umodzi wa miliri yoopsa kwambiri. Muliriu, kubwera ngati chilango cha machimo a onse amene sakhulupilira mwa Mulungu, udzasandutsa akasupe a madzi mmagazi ndi kuwapanga kukhala chosatheka kuti akhale mdzikoli lapansi. Mulungu adzasandutsa akasupe onse a madzi ndi mitsenje padzikoli lapansi mmagazi. Muliriu, naonso, ndi chiweruzo chopeerekedwa ku anthu adziko lapansi ngati dipo ndiponso chilango cha kususana kwao ndi Mulungu, amene anawapatsa madzi, mudzu wa moyo wonse.

Cifukwa cimene Mulungu adzabweretsera muliriu pa onse amene akhala ali kususana ndi Iye ndi cifukwa chakuti iwo anapha oyera ndiponso aneneri Ake pamene anali padzikoli lapansi. Awa ndi amene sanakane kukhulupilira mwa Mulungu ngati Mulungu kokha, komanso anasusana ndi Iye mogwirizana ndi Wosusa Khristu.

Odzaza ndi mphamvu ya Wosusa Khristu, amene asusana ndi chikondi cha Mulungu mdzikoli lapansi adzadzunza ndi kupha oyera a Mulungu okondedwa kwambiri ndi atumiki Ake. Onse amene tsopano sakhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu, umene Ambuye anthu anatipatsa kuti aombole anthu adzikoli lapansi kuchoka ku uchimo, adzapha oyera ambiri ndi aneneri a mnthawi yomaliza ndi kukhetsa magazi awo. Choncho Mulungu adzathira muliri Wake wachitatu padzikoli lapansi pamene adani Ake akukhala, adzasandutsa madzi ake, mudzu wa moyo wonse, mmagazi, choncho ndimene adzawaonongera.

Ichi ndi chiweruzo cha Mulungu, ndipo cifukwa cha ichi oyera mmtambo onse adzakondwera. Cifukwa nciani? Cifukwa ndi chiweruzo Chake choperekedwa kwa adani Ake amene anapaha oyera, Mulungu adzabwezera imfa ya oyera pa iwo. Choncho, oyera ndi atumiki a Mulungu sayenera kuopa, koma mmalo mwake ateteze chikhulupiliro chao mwa Ambuye Mulungu, ndi kuyangana pa malonjezano a Mulungu ndi mphamvu Yake ngati akumana ndi kuphedwa kwao.

 

Ndime ya 8-9: Mngelo wachinayir anathira mbale yake padzuwa. Ndipo dzuwa linaloledwa kutenthas anthu ndi moto. Choncho anthu anapsa ndi kutentha kwakukulu. Koma iwo ananyoza dzina la Mulungu, amene ali ndi ulamulirou pamiliri imeneyi, ndipo sanalape kuti amupatse ulemerero.

Monga mmene mngelo wachinayi akuthira muliri wa dzuwa, anthu adzapsa mpaka kufa cifukwa ndi kutentha kwake. Mulungu adzabweretsa muliri wotentha kwa dzuwa ku amene akhala ali kususana Ndi Iye. Cifukwa dzikoli lidzungulira dzuwa, kuti dzuwa linatsemphana ndi dzuwa ndi kufendelera kudzuwa ngakhale mtundu waung’ono, okhalamo ake onse akanapsa mpaka kufa. Choncho, ngati muliriu wachinayi wathiridwa, anthu okhalabe padzikoli lapansi onse adzadzunzidwa ndi kutentha.

Komabe iwo sadzalapa uchimo wao osusana ndi Mulungu. cifukwa nciani? Cifukwa posusana ndi uthenga wa madzi ndi Mzimu, iwo anagamulidwa kale kuchionongeko. Mwamsanga mmene zingathekere, choncho, wina aliyense tsopano ayenera kukonza chikhulupiliro chao cimene chingawalole kuthawa kuchoka ku mkwiyo wa Mulungu. chikhulupilirochi ndi kukhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu kukhala chikhulupiliro cha wina. Wina aliyense choncho ayenera kukhuluplira mchoonadi cha madzi ndi Mzimu.

 

Ndime ya 10-11: Mngelo wachisanu anathira mbale yake pampando wachifumu wa chilombo. Pamenepo ufumu wake unachita mdima, ndipo anthu anayamba kudziluma malilime chifukwa cha ululu. Koma iwo ananyoza Mulungu wakumwamba chifukwa cha ululu wawo ndi zilonda zawo, ndipo sanalape ntchito zawo.

Muliri wa mbale ya chisanu ndi umene udzabweretsa mdima ndiponso kuwawa. Kuchoka pa muliriru, anthu adzasheta malilime awo cifukwa cha kuwawa ndi kudzunzidwa kwake. Mulungu adzaonetsetsa kuti abwezera madzunzo a oyera pa iwo mwakawiri ndi kuwawa kwakukulu.

Mulungu adzawaoanga kuti adzunzidwe, mmawu ena, kwakukulu monga mmene oyera adzunzidwira poyamba. Ndipo komabe iwo adzanyozabe Mulungu ndipo sadzalapa, ngakhale kuti ali kudzunzidwa ndi zilonda zawo. Choncho, iwo adzalandira chilango chosatha cha gehena ndi moto oyaka ndiponso sulufule.

 

Ndime ya 12: Mngelo wa 6 anathira mbale yake pamtsinje waukulu wa Firate, ndipo madzi ake anauma, kuti njira ya mafumu ochokera kotulukira dzuwa ikonzedwe.

Muliri wa mbale ya 6 othiridwa ndi Mulungu ndi muliri wa njala umene udzaumitsa Mtsinje wa Efirate. Anthu adzakumana ndikudzunzidwa kwakukulu kuchoka ku muliriu. Muliri wa njala ndi muliri oopsa kwambiri ku moyo wa wina aliyense. Muliriu, umene udzathiridwa pa onse amene anakana uthenga wa madzi ndi Mzimu wopatsidwa ndi Ambuye, umationetsa mmene chilili kukulu chilango cha onse amene anakana chikondi cha Mulungu ndiponso kususana ndi Iye. Pomaliza, asilikari a Mulungu a Kumwamba ndi asilikari a Satana a padzikoli lapansi adzamenya nkhondo yomalizira pa malowa omenyerapo nkhondo. Satana ndi omusatira Ake, chotero, adzamangidwa ndipo adzaonongedwa ndi Mulungu.

 

Ndime ya 13: Kenako ndinaona mauthenga atatu onyansa ouziridwa, ooneka ngati achule, akutuluka m’kamwa mwa chinjoka, m’kamwa mwa chilombo, ndi m’kamwa mwa mneneri wonyenga.

Ndimeyi imationetsa kuti nchito za mzimu yoipa ndi ziwanda zochokera mkamwa mwa Satana, Chilombo Chake, ndi aneneri achinyengo. Nchito za ziwanda zidzagonjetsa dziko lonse lapansi ngati nthawi yake yomaliza yafika pafupi. Ziwanda zidzasocheretsa anthu powatsogolera kuchionongeko pochita zoziziswa ndiponso ziwonetsero kupyolera mwa Satana, aneneri achinyengo, ndiponso mwa Wosusa Khristu. Dziko la nthawi zomaliza choncho lidzakhala dziko la ziwanda. Koma dziko lawo lidzabweretsedwa komalizira kwake ndi miriri yam bale zothiridwa ndi Yesu Khristu ndi kubwera Kwake kwa chiwiri.

 

Ndime ya 14: Kwenikweni amenewa ndi mauthenga ouziridwa ndi ziwanda ndipo amachita zizindikiro. Mauthengawo akupita kwa mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti awasonkhanitsire pamodzi kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.

Mizimu ya ziwanda idzakhulumiza mitima mafumu onse a mdziko lonse lapansi kuti asonkhane pamalo amodzi kotero kuti amenyane ndi Mulungu. mdziko la nthawi zomaliza, mtima wa wina aliyense udzakokedwa mizimu ya ziwanda, ndipo iye choncho adzasanduka mtumiki wa Satana kuchita nchito za Mdyerekezi.

 

Ndime ya 15: “Taona! Ndikubwera ngati mbala. Wodala ndiye amene akhalabe maso ndi kukhalabe chivalire malaya ake akunja, kuti asayende wosavala anthu n’kuona maliseche ake.”

Ambuye adzabwera padzikoli lapansi ngati mbala, ndipo onse amene ateteza chikhulupiliro chao ndi kulalikira uthenga Wake mpaka pothiridwa kwa miriri yam bale zisanu ndi ziwiri ndi odalitsika kwakukulu. Ambuye athu amauza oyera okhala mnthawi zomaliza za dziko lapansi kuti iwo ayenera kukhala mwa chikhulupiliro mu uthenga wa madzi ndi Mzimu wopatsidwa ndi Iye ndipo kuti ateteze chikhulupilirochi mpaka tsiku lawo lomaliza. Onse amene ateteza chikhululiro chao mwa Ambuye isanathiridwe miliri Yake ya mbale zisanu ndi ziwiri adzalandira mphoto zazikulu kuchokera kwa Iye. Ambuye athu adzabweransodi kuti adzapeze onse amene pa iwo Iye adzaika madalitso Ake.

 

Ndime ya 16: Ndipo anawasonkhanitsa pamodzi, kumalo amene m’Chiheberi amatchedwa Haramagedo.

Baibulo limenenera kuti nkhondo yomaliza pakati pa Satana ndi Mulungu idzamenyedwera pa malo otchedwa Haramagedo. Koma cifukwa Mulungu ndi wamphamvuyonse, Iye adzagonjetsa Satana ndi kuponya Chilombo mng’anjo ya moto ndi sulufule. Tiyenera kudzindikira kuti Satana nthawi zonse akhala osocheretsa, ndipo tiyenera kusunga chikhulupiliro chathu mwa Ambuye mokhulupirika mpaka pa tsiku limene tidzaimira pamaso pa Mulungu.

Ndime ya 17-21: Ndiyeno mngelo wa 7 anakhuthulira mbale yake pampweya. Atatero, kunamveka mawu ofuula kuchokera m’malo opatulika, kuchokera kumpando wachifumu, akuti: “Zachitika!” Pamenepo kunachitika mphezi, kunamveka mawu, ndipo kunagunda mabingu. Kunachitanso chivomezi chachikuluu chimene sichinachitikepo chikhalire anthu padziko lapansi, chivomezi champhamvu kwambiri, chachikulu zedi. Pamenepo mzinda waukulu unagawika zigawo zitatu, ndipo mizinda ya mitundu ya anthu inagwa. Ndiyeno Mulungu anakumbukira Babulo Wamkulu, kuti amupatse kapu yokhala ndi vinyo wa mkwiyo wake waukulu. Komanso, chilumba chilichonse chinathawa. Ngakhale mapiri sanapezeke. 21 Ndipo matalala aakulu, lililonse lolemera pafupifupi makilogalamu 20, anagwera anthu kuchokera kumwamba. Anthuwo ananyoza Mulungue chifukwa cha mliri wamatalalawo, pakuti mliriwo unali waukulu modabwitsa.

Monga mmene Mulungu akuthira muliri wa mbale ya 7 mmtambo, kugunda ndi kufulasha kwa mphenzi kudzaononga mtambo, pamene chivomezi ndi matalala aakulu, amene akalibe kuonekapo ndikale lomwe, zidzakhuza dzikoli lapansi. ndi zionongekozi, dziko loyamba lidzazimiririka kosatsiya chidzindikiro chilichonse. Zitatha zimenezi, oyera adzakhala mu ulemerero ndi Yesu Khristu mdzikolo latsopano kwa zaka chikwi chimodzi zikubwera.

Ngati zaka chikwi chimodzi zapita ndipo nthawi yakwana yokwaniritsa malonjezo a Mulungu ya Kumwamba ndi Dziko lapansi la Tsopano a oyera yabwera, Mulungu adzapanga dziko loyamba kuzimiririka ndi kupatsa oyera kumwamba kwa chiwiri ndi dziko lapansi. Ndiyeno oyera adzakhala ndi Mulungu Kumwambaku kwa Tsopano ndi Dzikoli lapansi kwa muyaya. Oyera ayenera kukhulupilira kuti mu Ufumu wa Khristu kwa zaka chikwi chimodzi ndipo ndiyeno kukhala kwa muyaya mu ulemerero wa Kumwamba Kwake kwa Tsopano ndi Dziko lapansi. Iwo ayenera kukhala muchiyembekezocho, kuyembekezera kubweranso kwa Ambuye.