Sermons

[16-2] < Chivumbulutso 16:1-21 > Cimene Muyenera Kuchita Kuthiridwa kwa Mbale 7 Kusanachitike Ndi…< Chivumbulutso 16:1-21 >


Za miliri ya mbale 7, muliri woyamba ndi uja wa zilonda, muliri wachiwiri ndi uja osandutsa nyanja mmagazi, ndipo wachitatu ndi wakuti madzi kusanduka magazi, muliri wachinayi, ndi uja pamene anthu adzaotchedwa mpaka kufa ndi kutentha kwa dzuwa.

Ndime tawerengayi imatiuza kuti, “Mngelo wachinayi anathira mbale yake padzuwa. Ndipo dzuwa linaloledwa kutentha anthu ndi moto. Choncho anthu anapsa ndi kutentha kwakukulu.” Ichi chimatiuza kuti Mulungu adzabweretsa pafupi dzuwa padzikoli lapansi ndi kuotcha zamoyo Zake mpaka imfa. Ngati Mulungu alora ichi kuchitika, kulibe wina aliyense adzakwanitsa kuthawa kuchoka kukutenthaku kwa dzuwa, ngakhale kuti wina angakumbe dzenje lolowa kunsi ndi kubisala kumeneko. Kapena kuyasha chisulo chozizimitsira chapamwamba chokonzedwera muliriu iwo sadzakwanitsa kuleketsa muliriu wa Mulungu. Onse aiwo sadzakhala ndi funiro koma kufa chabe. 

Tingalingalirepo pa zimene zidzachitika pa iwo ngati muliriu wabwera—zikumba zawo zidzafunduka; thupi lawo lamkati lidzakhala lophikidwa, kupwanyika ndiponso kuola. Wina aliyense adzafa ndi zilonda za kuzikumba. 

Ndipo komabe, ngakhale iwo ali kuotchedwa mpaka kufa ndi kutentha kwa dzuwa, anthu sadzalapabe machismo awo. Muliri wa Mulungu ndioopsa, koma choncho ndi anthuwa amene akukana kulapa ngakhale ali kupita mu muliriu. Monga mmene akukanira kulapa, miliri ya Mulungun idzapitilizabe.

Ndime tawerenga ikuti, “Mngelo wachisanu anathira mbale yake pampando wachifumu wa chilombo. Pamenepo ufumu wake unachita mdima, ndipo anthu anayamba kudziluma malilime chifukwa cha ululu. Koma iwo ananyoza Mulungu wakumwamba chifukwa cha ululu wawo ndi zilonda zawo, ndipo sanalape ntchito zawo.” Ngati tayangana padziko la matsiku ano, sitimaona nambala yosawerengeka ya anthu amene ayenera kuweruzidwa ndi Mulungu tsopanoli? Koma cifukwa Mulungu akusunga mkwiyo Wake mkudekha mtima, iwo mpaka tsopanoli sakuweruzidwa. Choncho, ngati iwo anafa kosakhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu wopatsidwa ndi Yesu Khristu, adzabweretsedwanso ku moyo ndi Mulungu mu mathupi osafa, ndipo adzakumana ndi kudzunzidwa mu moto woyakha-kwa muyaya wa gehena. 

Ngati ichi chachitika, anthu adzafuna kufa, monga mmene kudzunzidwa kwao kudzakhala kwakukulu kotero kuti iwo apilire. Koma kudzunzidwa kwa gehena kumatha kwa muyaya. Nthawi idzabwera pamene onse amene ayenera kuweruzidwa ndi Mulungu adzafuna kuti afe, koma imfa idzawathawa, cifukwa Mulungu adzawateteza kuchoka kukufa kotero kuti Iye awaweruze kwa muyaya. 

Muliri wa 6 ndi wa nkhondo ya Haramagedo. Ndipo muliri wa 7 ndi muliri womaliza ndiponso wotsilizitsa wa chivomezi chachikulu ndiponso matalala aakulu. 

Ndime ya 17-21 imatiuza kuti, “Ndiyeno mngelo wa 7 anakhuthulira mbale yake pampweya. Atatero, kunamveka mawu ofuula kuchokera m’malo opatulika, kuchokera kumpando wachifumu, akuti: “Zachitika!” Pamenepo kunachitika mphezi, kunamveka mawu, ndipo kunagunda mabingu. Kunachitanso chivomezi chachikuluu chimene sichinachitikepo chikhalire anthu padziko lapansi, chivomezi champhamvu kwambiri, chachikulu zedi. Pamenepo mzinda waukulu unagawika zigawo zitatu, ndipo mizinda ya mitundu ya anthu inagwa. Ndiyeno Mulungu anakumbukira Babulo Wamkulu, a kuti amupatse kapu yokhala ndi vinyo wa mkwiyo wake waukulu. Komanso, chilumba chilichonse chinathawa. Ngakhale mapiri sanapezeke. Ndipo matalala aakulu, lililonse lolemera pafupifupi makilogalamu 20, anagwera anthu kuchokera kumwamba. Anthuwo ananyoza Mulungue chifukwa cha mliri wamatalalawo, pakuti mliriwo unali waukulu modabwitsa.” 

Ndime ya pamwambapa imatiuza kuti monga mmene Mulungu ali kuthira mbale ya 7, chivomezi chachikulu chidzakhuza dziko, dziko lonse lidzagawikana zigawo zitatu, ndipo manyumba oimililabe mdzikoli onse adzagwetsedwa, kusatsiyako ndinga ndi imodzi ya izo yosagwetsedwa. Monga mmene dzikoli ndilogonjera pansi pa ukari wa Mulungu, zilumba zonse ndiponso maluphiri adzazimiririka. 

Kodi Maluphiri a Himalaya adzakhalabe oimilira ngati ichi chachitika? Ndithudi ai! Maluphiri onse aatali adzazimiririka pamaso pamene pa amoyo. Luphiri lilonse mdzikoli lapansi lidzasungunuka kosatsiyako ndi chidzindikiro. Ndimeyi imatiuzanso kuti matalala aakulu, lina lilonse lolemela ngati ma paundi 100 (45kg), adzagwera padzikoli lapansi. Kodi kudzakhala wina aliyense ndi moyo mu zivomezizi ndi matalala? 

Chivumbulutso 18 imatiuza kuti mkwiyo wa mulungu umabweretsedwa pa onse amene sanakhulupilire mwa Iye ndi amene asula Mawu Ake. Anthu ena mdzikoli lapansi akunena kuti, nga ndipamene anali muuzimu, “Sindidzagonjera pa mkwiyo wa Mulungu, kapena Ine ndidzaweruzidwa ndi Iye.” Choncho, chiweruzo cha Mulungu chibweretsedwa makamaka pa mtunduwu wa anthu amene ndi odzaza ndi kudzikuza ndi kudzikweza kwao. Tiyenera kukhulupilira kuti dzikoli lapansi lidzazimiririka ngati lakhuzidwa ndi miliri ya mbale 7 yothiridwa ndi Mulungu. Tiyenera Kukhala ndi Chikhulupiliro mu Mawu a Mulungu.


Mulungu amatiuza kuti dzikoli lidzazimiririka. Choncho dzikoli silidzatha kwa muyaya. Choncho, onse amene ali kukumana ndi kufenderera pafupi ndi kumapeto ayenera kukhulupilira mchoonadichi ngakhalenso molimbika kwamiri ndi kupeza chikhulupiliro chao cha muuzimu. Anthu choncho a mdzikoli lapansi ayenera kuuka mtulo twao twa kumzimu. Si Ndikudziwa mtundu wa chikhulupiliro cimene inu mwakhala mu umoyo wanu kuchoka kumbuyoku, koma tsopano ndi nthawi kuti inu muike nzeru zanu ku zimene zidzakhala zili kuchitika mnthawi zomaliza, ndipo ndikuuka ndiponso kukhulupilira. Choncho inu muyenera kukhala ndi kudziwa kwenikweni kwa miliri imene inaneneredwa mu Buku la Chivumbulutso, ndipo muyenera kukhala maso. 

Ambuye anatiuza kuti dzikoli tsopanopa lidzakhala pansi pa miliri ya mbale za Mulungu. Choncho, tiyenera kuyembekezera Ambuye pamene tilikupitiliza kulalika uthenga, ngakhale kuti anthu saulandira bwino. 

Tsopano mpata wa dzikoli uli pampenu-mpenu. Dziko la tsopanoli likuonetsedwa ku mitundu yonse ya zoopseza, kuchoka kuchoopsezo cha nkhondo mpaka kuchioopseza cha masintha sintha a mphepo, chionongeko cha zolengedwa, kuchulukitsa mkangano wa za chikhalidwe, ndiponso mitundu yonse ya matenda. Choncho Mulungu amatiuza kuti nthawi ya tsopanoyi ili ngati nthawi ya Nowa, ngati nthawi ino ili ngati nthawi ya Nowa, chitanthauza chabe kuti dzikoli lapansi tsopano la lowa mmatsiku ake omaliza. Chidzindikiro cha nthawi zomaliza ndi chakuti anthu adzakhala ndi chidwi mu zinthu za thupi zokha, monga kudya, kumwa, kukwatira kwatira, ndi zina zogwizana zopandapache. Choncho iwo ayenera kuweruzidwa ndi Mulungu. mnthawi ya Nowa, namonso, anthu otero sanalabadire zimene Nowa anali kuwauza, ndipo tero onse anaonongedwa, kuchosako Nowa ndi banja lake la asanu ndi atatu. Dziko likubwera lidzakhala ngati dzikoli chimodzimodzi. 

Pafupi-fupi zinthu zonse zimene Mulungu analonjeza zakwanilitsidwa kulingana ndi mmene Baibulo inalembela. Pa zimenezi, zokwala ma peresenti 5 zakhalabe kuti zikwanilitsidwe, koma zambiri za izo zakwanilitsidwa kale. Mawu a chipulumutso ndiponso achiombolo olonjezedwa ndi Ambuye onse naonso akwanilitsidwa kale. Mu Mawu a Mulungu, chiweruzo chokha chosungidwira onse amene sakhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu chakhalabe. Ndipo ku oyera obadwa-mwatsopano, ndi Ufumu wa zaka Chikwi chimodzi ndiponso Dziko lapansi lokha, mmene olungama adzalowa ndi kukhala mmenemo, kuwayembekeza iwo. 

Mulungu ndi wachifundo, ndipo Iye aimilira kumbali ya olungama. Koma, ku onse amene ayenerera mkwiyo Wake, Mulungu adzabweretsadi mkwiyo Wake pa iwo, pamene ku onse amene ayenerera chifundo Chake, Iye adzaikapodi chifundo Chake. 

Kodi niliti pamene miliriyi idzachitika? Miliri yam bale 7 idzabwera kuphedwa kwa oyera kutapita, monga mmene chidzindikiro cha 666 chikakamizidwa padzikoli lapansi ndipo kukanidwa ndi oyera. Miliri itatha kudzabwera chiukitso choyamba, Ufumu wa zaka Chikwi chimodzi, ndiponso chiweruzo chomaliza cha Yesu okhala pampando oyera wachifumu. Ichi chidzasatiridwa ndi kutsegulidwa kwa Ufumu wosatha wa Kumwamba. Kupyolera mu Baibulo, tiyenera kupeza kudziwa ulamiliro wa uzimu wa Mulungu. 

Kodi inu mkhulupilira mchoona chakuti Yesu anaukanso ku akufa? Kodi inu mkhulupilira kuti Ambuye anapanga machimo onse a anthu kuzimiririka kupyolera mu ubatizo Wake ndi magazi? Ambuye athu anachotsa machimo a anthu ndi Ubatizo Wake ndi magazi, anaukanso ku akufa mmatsiku atatu, ndipo tsopano ali kukhala ku dzanja la manja la mpando wachifumu wa Atate. Choncho, machismo a onse amene akhulupilira mwa Yesu Khristu poyera poyera anazimiririka, ndiponso monga mmene Khristu anaukanso ku akufa, chotero ndi mmene iwo adzaukilanso. 

Choncho oyera adzalemekezedwa ndi Ambuye, koma pamene anali padzikoli lapansi, iwo naonso adzakumana ndi madzunzo ambiri cifukwa cha Ambuye. Koma madzunzo a nthawi ino si ayenerera kulinganiza ndi ulemerero umene umawayemekezera iwo, cifukwa ulemererou ndi chinthu chokha cimene chiyembekezera oyera obadwa-mwatsopano. Choncho oyera alibe ndi chowadetsa nkhawa cha zakutogolo. Cimene olungama ayenera kuchita chokha ndi kukhala miyoyo yawo yonse mu uthenga ndiponso mwa chikhulupiliro. Tiyenera kuzipereka pa nchito yopulumutsa miyoyo, ndipo tisasate dziko lapansi. Tiyeni Tipereke Miyoyo Yathu Yonse Kwa Mulungu


Ndili ndi nkhawa kuti pakhala wina pakati pathu amene angapandukire uthenga. Aliyense amene akupandukira uthenga wa madzi ndi Mzimu adzakana Ambuye iyeyekha pothera. Ngakhale kuti nndife ofooka, ngati timakhulupilira mu ndiponso timasatira uthenga wa madzi ndi Mzimu wokwanilitsidwa ndi Ambuye, tonse tidzakwanitsa kukhala mwa chikhulupiliro. Oyera sangakhale ndi nzeru ndi mphamvu zawo zokha. Kuti iwo akanachita tero, akanathera pa kupandukira chikhulupiliro chao ndi kukumana ndi chionongeko chao. Kuti tipewa ichi, tiyenera kukhala mwa chikhulupiliro. 

Kodi cifukwa nciani Ambuye adzalora anthu kulandira chidzindikiro cha 666? Uku ndi kupatula tirigu ku mankhusu. Asanalora oyera kukwatulidwa, chinthu choyamba cimene Mulungu adzachita ndi poyera-yera kupatula tirigu kuchoka ku mankhusu. 

Kuli nkhondo ya uzimu imene idzamenyedwa ndi oyera. Choncho, oyera sayenera kupewa kumenyana ndi adani a Mulungu. Ngati iwo aopa kumenyana ndi Satana, angalandire khofi lofanala kuchokera kwa Satana mmalo mwake. Choncho, oyera onse ayenera ndiponso angamenye nkhondo ya kuuzimu ngakhale pa iwo okha. Nkhondo zonse za kuuzimu zomenya oyera ndi zoyenerera. Kuti msatire Mulungu, oyera aliyense ayenera kumenya ndiponso kugonjetsa Satana ndi akapolo ake. 

Oyera ayenera kumenya cifukwa cha Ufumu wa Mulungu. Iwo ayenera kudzunzidwa cifukwa cha Ufumu wa Mulungu, ndi kuzondedwa ndi anthu adziko lapansi. Ku oyera amapatsidwa mpata kuti amenye nkhondo cifukwa cha Ambuye ndi chinthu chabwino icho chokha. Ngati mpatau omenya nkhondo mmalo mwa Mulungu unapatsidwa kwa inu, muyenera kumuthokoza Iye cifukwa cha umeneu. Nkhondo yotero ndi nkhondon yabwino, cifukwa ndi nkhondo ya chilungamo cha Mulungu. 

Mulungu amathandiza olungama. Si kuti kuli matsiku ambiri okhala mu miyoyo yathu, ndipo chiyembekezo change ndi pemphero langa ndi kuti tiyenera kukhala miyoyo yathu yokhalako kumenya nkhondo za muuzimu ndiponso kuchita nchito za muuzimu mpaka tikaime pamaso pa Ambuye. Palibbe kanthu pa zimene anthu adzikoli akulankhula za ife, tiyenera kumenya nkhondo za muuzimu, kubala zipatso za muuzimu, ndi kupereka zipatsozi pamaso pa Ambuye athu. Ngati tsiku lobweranso Ambuye labwera, tiyeni tose tiimilire pamaso pa Iye mokhulupirika. Ngati tsikuli labwera, Ambuye adzapuputa misozi zathu ndi kutilora kukhala mmalo amene si tidzaliranso, ngakhale kudzunzidwanso ndi zowawa, kapena kupezanso uchimo. 

Tiyeni tonse tikhale mwa chikhulupiliro, ndipo mwa chikhulupilirochi tiyeni tilowe mu Ufumu wa Mulungu.