Sermons

[17-1] < Chivumbulutso 17:1-18 > Kuweruzidwa kwa Hule Lokhala pa Madzi Ambiri< Chivumbulutso 17:1-18 >

“Mmodzi wa angelo 7 amene anali ndi mbale 7 aja, anabwera n’kundiuza kuti: “Bwera, ndikuonetsa chiweruzo cha hule lalikuluh lokhala pamadzi ambiri, limene mafumu a dziko lapansi anachita nalo dama, ndipo linaledzeretsa anthu okhala padziko lapansi ndi vinyo wa dama lake.” Mu mphamvu ya mzimu, mngeloyo ananditengera kuchipululu. Ndipo ndinaona mkazi atakhala pachilombo chofiira kwambiri, chodzaza ndi mayina onyoza Mulungu. Chinali ndi mitu 7, ndi nyanga 10. Mkaziyo anavala zovala zofiirira ndi zofiira kwambiri. Anadzikongoletsa ndi golide, ndi mwala winawake wamtengo wapatali, ndiponso ngale. M’dzanja lake, anali ndi kapu yagolide yodzaza ndi zonyansa ndi zinthu zodetsedwa zokhudzana ndi dama lake. Pamphumi pake panalembedwa dzina lachinsinsi lakuti: 

“BABULO WAMKULU, MAYI WA MAHULE NDI WA ZONYANSA ZA PADZIKO LAPANSI.” 

Ndipo ndinaona kuti mkaziyo anali ataledzera ndi magazi a oyera, ndiponso magazi mboni za Yesu. Nditamuona mkaziyo, ndinadabwa kwambiri. Koma mngelo uja anandifunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ukudabwa? Ndikuuza chinsinsi cha mkazi ameneyu, ndi cha chilombo chimene wakwerapo, chokhala ndi mitu 7 ndi nyanga10: Chilombo chimene waona, chinalipo, d tsopano palibe, komabe chili pafupi kutuluka kuphompho, e ndipo chidzapita ku chiwonongeko. Anthu okhala padziko lapansi akaona kuti chilombocho chinalipo, tsopano palibe, komabe chidzakhalapo, adzadabwa kwambiri. Koma mayina awo sanalembedwe mumpukutu wamoyo kuyambira pa kukhazikitsidwa kwa dziko. “Apa m’pamene pakufunika kuchenjera ndiponso kukhala ndi nzeru: Mitu 7 ikuimira mapiri 7, amene mkazi uja amakhala pamwamba pake. Palinso mafumu 7. Asanu agwa, imodzi ilipo, inayo sinafikebe. Koma ikafika, ikufunika kudzakhala kanthawi kochepa. Ndipo chilombo chimene chinalipo, koma tsopano palibe, n’chimenenso chili mfumu ya 8, koma yotuluka mwa mafumu 7 aja, ndipo ikupita ku chiwonongeko. “Nyanga 10 zimene unaona zija, zikuimira mafumu 10 amene sanalandirebe ufumu wawo. Koma adzalandira ulamuliro monga mafumu ndipo adzalamulira limodzi ndi chilombo kwa ola limodzi. Mafumuwa maganizo awo ndi amodzi, choncho adzapereka mphamvu zawo ndi ulamuliro wawo kwa chilombocho. Iwowa adzamenyana ndi Mwanawankhosa, koma pakuti iye ndiye Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu, Mwanawankhosayo adzawagonjetsa. Komanso oitanidwa aja, amene ali osankhidwa mwapadera ndi okhulupirika, nawonso adzagonjetsa naye limodzi.” Kenako mngeloyo anandiuza kuti: “Madzi amene wawaona aja, pamene hule lija lakhala, akuimira mitundu ya anthu, makamu, mayiko, ndi zinenero. Nyanga 10 waziona zija, komanso chilombo, zimenezi zidzadana nalo hulelo. Zidzalisakaza ndi kulisiya lamaliseche. Zidzadya minofu yake ndi kulinyeketsa ndi moto. Pakuti Mulungu anaika izi m’mitima yawo kuti zichite monga mwa maganizo ake, g kuti zikwaniritse maganizo awo amodzi, mwa kupereka ufumu wawo kwa chilombo, kufikira mawu a Mulungu atakwaniritsidwa. Ndipo mkazi amene unamuonayo akuimira mzinda waukulu umene ukulamulira mafumu a dziko lapansi.’” Kusanthula


Ndime ya 1: Mmodzi wa angelo 7 amene anali ndi mbale 7 aja, anabwera n’kundiuza kuti: “Bwera, ndikuonetsa chiweruzo cha hule lalikulu lokhala pamadzi ambiri,”

Titadziwa amene ndi hule, mkazi, ndi Chilombo cha mndime imene tawerenga ndichofunikira kuti timnasulire ndi kumvetsetsa za chapitala 17. “Hule” mndime ya 1 aimilira za chipembezo cha dziko lapansi, pamene “mkazi” aimilira dziko lapansi. “Chilombo,” mnjira ina, chiimilira Wosusa Khristu. “Madzi ambiri” aimilira ziphunzitso za Mdyerekezi. Mawu akuti, “ndikuonetsa chiweruzo cha hule lalikulu lokhala pamadzi ambiri,” amatiuza kuti Mulungu adzaweruza chipembezo cha dziko cimene chaimilira pa ziphunzitso zambiri za Satana.


Ndime ya 2: “limene mafumu a dziko lapansi anachita nalo dama, ndipo linaledzeretsa anthu okhala padziko lapansi ndi vinyo wa dama lake.”

“Dama” liimilira kukonda kwa dzikoli lapansi ndi zinthu zake kwambiri koposa kukonda Mulungu Iyeyekha. Kupanga zifaniziro za zinthu za dziko lapansi, ndi kudzilambira ndiponso kuzikonda ngati Mulungu mchoona zonsezi ndi mchitidwe wa dama. 

Mawu pamwamba akuti, “limene mafumu a dziko lapansi anachita nalo dama,” atanthauza kuti atsogoleri a dzikoli lapansi akhala miyoyo yoledzera ndi zipembezo za dzikoli lapansi, ndi kuti anthu onse a za dziko lapansi naonso okhala oledzera ndi machismo otero amene zipembezo za dziko lapansi zili kupereka. 


Ndime ya 3: Mu mphamvu ya mzimu, mngeloyo ananditengera kuchipululu. Ndipo ndinaona mkazi atakhala pachilombo chofiira kwambiri, chodzaza ndi mayina onyoza Mulungu. Chinali ndi mitu 7, ndi nyanga 10. 

Mawu akuti, “Mkazi atakhala pa Chilombo chofiira kwambiri,” amatiuza kuti anthu adzikoli lapansi adzagwirizana mtima yawo ndi uja wa Wosusa Khristu kuti adzunze ndi kupha oyera. Amationetsa kuti anthu a za dziko lapansi pothera adzakhala atumiki a mdani wa Mulungu, kugwira nchito za Satana pa ulamuliro wake. Chilombo ndi Wosusa Khristu amene akususa ndi Mulungu. wosusa Khristu amalamulira pa mafumu ambiri, ndiponso iye amalamuliranso mitundu yambiri ya dziko lapansi. 

Pokhala ozitukumula Wosusa Khristu sadzaopa kunyoza Mulungu ndi kutulutsa mawu ake ozitukumula. Iye adzanyoza Mulungu potulutsa mawu ozitukumula, kunena kuti iyeyekha ndi Mulungu kapena Yesu Khristu, ndipo iye adzazikweza iyeyekha pamwamba ngati Mulungu. mphamvu yake idzalamulira mafumu onse a dziko lapansi ndiponso pa mitundu yake yonse. 

Kuchokera mu mawu, “Chinali ndi mitu 7, ndi nyanga 10,” apa aimilira mafumu 7 a dziko lapansi, ndipo “nyanga 10” ziimilira mitundu 10 ya dziko lapansi. 


Ndime ya 4: Mkaziyo anavala zovala zofiirira ndi zofiira kwambiri. Anadzikongoletsa ndi golide, ndi mwala winawake wamtengo wapatali, ndiponso ngale. M’dzanja lake, anali ndi kapu yagolide yodzaza ndi zonyansa ndi zinthu zodetsedwa zokhudzana ndi dama lake.

Ndi mawu akuti, “Mkaziyo anavala zovala zofiirira ndi zofiira kwambiri, ndi mwala winawake wamtengo wapatali, ndiponso ngale,” ndime imatiuza kuti zipembezo za dziko lapansi, zopangidwa ndi Wosusa Khristu, adzaganizira iye kukhala ngati mfumu yawo. Choncho, iwo adzachiona ngati choyenera kuti onse amene asusana ndi iwo ayenera kuphedwa, ndipo mchoona iwo idzakwanilitsa malingaliro awo kupyolera mu machitidwe awo oukira oyera. 

Ndipo kukongoletsa dzikoli lapansi ngati ufumu osatha wa chikondwerero, iwo adzazikongoletsa iwo okha ndi golide wa dziko lapansi, ndi miyala ya mtengo wa pamwamba ndi ngale. Koma chikhulupiliro chao ndichofunitsitsa chabe za unyinji wa zokondweretsa thupi zimene angakhale nazo pamene okhala padzikoli lapansi. cifukwa pamene Mulungu anaona padzikoli lapansi Iye anangoona chabe dziko lapansi lodzaza ndikudetsedwa ndi machimo awo, onse adzaoneka nagti onyansa pamaso pa Iye. 


Ndime ya 5: Pamphumi pake panalembedwa dzina lachinsinsi lakuti: “BABULO WAMKULU, MAYI WA MAHULE NDI WA ZONYANSA ZA PADZIKO LAPANSI.” 

Ngakhale anthu a zipembezo angayetse kuzikongoletsa iwo okha ngati mfumukazi. Mchoona adzavumbulutsidwa kukhala ngati hule. Mnjira ina, dzina lake, “Babulo Wamukulu,” limationetsa kudzitukumula, wadama, ndipo mkhalidwe wopondeleza wa hule, pamene mawu akuti “mayi,” mnjira ina, amationetsa kuti mphamvu zonse za Wosusa Khristu kulingana ndi mbiri yake zinachokera ku dziko lapansi ilo lokha, ndi kuti dziko lapansi ndi mudzu wa mtundu uliwonse wa dama ndiponso chiphuphu. 

Ngakhale kuti dzikoli ndilokongoletsedwa ndi majewli onyezimira ndiponso okongola, Wosusa Khristu amene asusana ndi Mulungu ndipo akugwira nchito mmitima ya anthuwa a dziko lapansi adzagwira nchito ngati mayi wao. Choncho, Ambuye Mulungu wathu anakonza kuwaononga onse ndi miliri Yake yaikulu ya mbale 7.


Ndime ya 6: Ndipo ndinaona kuti mkaziyo anali ataledzera ndi magazi a oyera, ndiponso magazi mboni za Yesu. Nditamuona mkaziyo, ndinadabwa kwambiri. 

“Oyera” apa aimilira anthu achikhulupiliro mnkhani yonse ya M’pingo umene unakhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu wopatsidwa ndi Yesu Khristu. Mawu akuti “Ophedwa a Yesu” aimilira aja pakati pa oyera anachitira umboni choonadi kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu ndiponso ndi M’pulumutsi wao, ndiponso makamaka amene anaphedwa kuti ateteze chikhulupiliro chao. 

Ndimeyi imalankhula kwambiri kuti amene adzazunza ndi kupha oyera ndi anthu a zipembezo za dzikoli lapansi. adzachita zoipa zotero ngati atumiki a mphamvu a Wosusa Khristu.

Yohane apa akuti iye atamuona mkaziyo, iye “anadabwa ndi kudabwa kwakukulu.” Dzikoli ndi dzikodi loopsa. Oyera palibe cimene anachita kuti alikhuze, komabe dzikoli lipanga chiwembu ndi Wosusa Khristu ndi kupha oyera ambiri. Kodi dziko silingakhale chinthu china koma kukhala lachilendo? Zinthuzi zidzabweretsedwadi ku oyera ndi anthu a dzikoli lapansi. Cifukwa dzikoli lapansi lili paulamuliro wa Wosusa Khristu, anthu ake, ngati atumiki ake, adzagwira ndi kuwapha oyera. 

Choncho iwo adzaonekadi achilendo kwambiri kwa ife. Ngati tayangana pa anthu a za dziko lapansi, kodi iwo mchoona saoneka ngati mwina ndi alendo? Ngati anthu anapangidwa muchifaniziro cha Mulungu, kodi iwo angakhalenso bwanji atumiki a Wosusa Khristu ndi kupha anthu—osati anthu ena ali onse, koma anthu osawerengeka amene akhulupilira mwa Mulungu? Ndi cifukwa chakuti dzikoli lapansi ndi mtumiki wa Satana. 


Ndime ya 7: Koma mngelo uja anandifunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ukudabwa? Ndikuuza chinsinsi cha mkazi ameneyu, ndi cha chilombo chimene wakwerapo, chokhala ndi mitu 7 ndi nyanga10.” 

“Mkazi” apa aimilira anthu adzikoli. Ndimeyi imatiuza kuti Chilombo, chotchedwa Wosusa Khristu, chidzalamulira pa mafumu onse a mdziko lapansi ndiponso pa mitundu yake, ndipo ngakhale kuti iwo adzagwira nchito yosusa ndi Mulungu, yodzunza oyera, ndipo yokuwapha. “Chinsinsi cha chilombo” chiimilira khalidwe la Wosusa Khristu, kukhala pa kulamulilidwa ndi Satana. Ndipo iye adzasandutsa mitundu ya dzikoli lapansi kukhala yake yake. 

Anthu a mdzikoli lapansi, otsoholeledwa ndi Wosusa Khristu, adzathera pokhala zida za Satana zophera chiwerengero chachikulu cha anthu a Ambuye. Dzikoli lapansi ndi Wosusa Khristu ndi zida za Satana zobisa kumaso kwa tsopano. Koma ngati zaka zoyamba zitatu ndi hafu za Chisautso Chachikulu zapita, iwo adzauka ndi kupha oyera. 

Wina angafunse kodi ichi chidzakhala chotheka motani, pamene dzikoli lapansi lili ndi anthu ochenjera, ophunzira, ndiponso obvala bwino, kuchokera ku adzandale mpaka ku ophunzitsa mpaka ku mafilosofa mpaka ku a ma PhD. Koma cifukwa dziko lapansi lidzagwirizana ndi Wosusa Khristu, zonse zinthuzi, kuphatikizapo kupha kwa oyera, zidzakhala zotheka. Choncho, kuti dzikoli lapansi lidzazipereke kwa Wosusa Khristu ndi kupha oyera ndi kiyi wothetsera chinsinsi cha Wosusa Khristu.

Ndime ya 8: “Chilombo chimene waona, chinalipo, tsopano palibe, komabe chili pafupi kutuluka kuphompho, ndipo chidzapita ku chiwonongeko. Anthu okhala padziko lapansi akaona kuti chilombocho chinalipo, tsopano palibe, komabe chidzakhalapo, adzadabwa kwambiri. Koma mayina awo sanalembedwe mumpukutu wamoyo kuyambira pa kukhazikitsidwa kwa dziko.”

Ndimeyi imatiuza kuti Wosusa Khristu anapezeka pakati pa mafumu anthawi zakale, ndipo kuti ngakhale kuti tsopano sali mdziko lapansi, iye adzatulukira mdziko lapansi mtsogolo posachedw. Imatiuza kuti anthu adziko lapansi adzakhala odabwa kwambiri ngati aona Wosusa Khristu akuonekera ndi kupha oyera. 

Wosusa Khristu adzakwanilitsa zolinga zake potengako mbali mzandale za tsopano za dziko lapansi. I adzapitilizabe kukhala wachinsinsi ku anthu a dzikoli lapansi ndipo koma iye adzasankhidwa ngati odabwitsa. Cifukwa iye adzatenge mabvuto ambiri a zandale, za chuma, zamwambo, ndiponso za chipembezo mdzikoli lapansi ndi kuyathetsa onse mu mphamvu zake, anthu adzaganiza za iye ndipo adzamusata iye ngati Yesu Khristu amene adzabweranso pa nthawi zomaliza. Choncho iye adzakhalabe odabwitsa pamaso pa anthu adziko lapansi. 


Ndime ya 9: “Apa m’pamene pakufunika kuchenjera ndiponso kukhala ndi nzeru: Mitu 7 ikuimira mapiri 7, amene mkazi uja amakhala pamwamba pake.”

Ndimeyi imatiuza kuti Wosusa Khristu adzakhazikitsa malamulo ake kuti alamulire pa anthu a dziko lapansi ndi kuwasandutsa malamulowa mmthupi la kulamulira kwake kuti akwanilitse zolinga zake. Cifukwa cymene anthu a dziko lapansi adzagwirizana ndi kubwera pansi pa lamulo la Satana polandira chidzindikiro cha Wosusa Khristu, ndi kususana ndi Mulungu ndiponso oyera Ake, kuika chikhupilira chao mu mphamvu ya malamulo opangidwa ndi Wosusa Khristu.


Ndime ya 10: “Palinso mafumu 7. Asanu agwa, imodzi ilipo, inayo sinafikebe. Koma ikafika, ikufunika kudzakhala kanthawi kochepa.”

Ndimeyi imatiuza kuti mafumu amene asusana ndi Mulungu adzapiliza kutulukira mdzikoli lapansi, monga mmene mafumu otero anaukira n’kale lomwe. Ngati nthawi yomaliza ya Chisautso Chachikulu yabwera, mtsogoleri wa dzikoli lapansi adzauka ngati Wosusa Khristu ndi kupha oyera. Koma kudzunzidwa kwa mtsogoleri wa dzikoli lapansi, amene adzakhala Wosusa Khristu, kudzatha chabe kwa ka nthawi kang’ono pamene kudzaloredwa ndi Mulungu.

 

Ndime ya 11: “Ndipo chilombo chimene chinalipo, koma tsopano palibe, n’chimenenso chili mfumu ya 8, koma yotuluka mwa mafumu 7 aja, ndipo ikupita ku chiwonongeko.” 

Ichi chimatiuza kuti Wosusa Khristu obwera mdzikoli lapansi adzauka ngati umodzi wa mafumu omaliza a mdziko lapansi. Ngati Wosusa Khristu aonekera kutuluka mkati mwa mafumu a mdziko lapansi, anthu ambiri a mdziko lapansi adzamusatira Iye, monga mmene iye, atalandira mzimu wa Chinjoka, adzaonetsa mphamvu ngati Mulungu kuchita zionetsero ndiponso zodabwitsa. Atumiki ndiponso oyera a Mulungu naonso adzaphedwa ndi Wosusa Khristu, koma zinthu zonsezi zidzachitika kwa kanthawi kang’ono pamene kadzaloredwa ndi Mulungu. zitatha zinthu zimenezi, Wosusa Khristu adzamangidwa mdzenje lolowera kuphompho, ndipo ndiyeno kuponyedwa mu gehena wa moto, kosamasulidwa kuchokera mmenemo. 

Ndime ya 12: “Nyanga 10 zimene unaona zija, zikuimira mafumu 10 amene sanalandirebe ufumu wawo. Koma adzalandira ulamuliro monga mafumu ndipo adzalamulira limodzi ndi chilombo kwa ola limodzi.”

Ndimeyi imatiuza kuti mitundu 10 idzaika mphamvu zake pamodzi kotero kuti ilamulire dziko lonse lapansi. Mitunduyi 10, itagwirizana chonchi, idzaika mphamvu zake pa dziko lapansi ndi Wosusa Khristu kwa kanthawi kang’ono. Koma ndime imatiuzanso kuti mafumuwa a dziko lapansi sanalanirebe ufumu olamulilidwa ndi Wosusa Khristu. Mtsogolo posachedwapa, chotero, mafumuwa a dziko lapansi adzalamulira limodzi ndi Chilombo ngati mafumu a mdima kwa kanthawi kakang’ono. Koma kulamulira kwao kudzatha kwa nthawi yochepa chabe, ndipo choncho, adzalamulira pa mphamvu za mdima kwa nthawiyi yaing’ono ya nthawi. 


Ndime ya 13: “Mafumuwa maganizo awo ndi amodzi, choncho adzapereka mphamvu zawo ndi ulamuliro wawo kwa chilombocho.”

Ngati nthawi yabwera, mafumu a dzikoli lapansi adzapereka mphamvu zawo ndi ulamuliro wawo kwa Wosusa Khristu. Panthawiyi, M’pingo wa Mulungu, oyera ake, ndi atumiki Ake adzazunzidwa kwakukulu ndi Wosusa Khristu ndi kuphedwa. Koma Wosusa Khristu iyeyekha adzaonongedwa ndi mphamvu ya ndiponso ulamuliro wa Yesu Khristu ndiponso ndi lupanga la Mawu otuluka mkamwa Mwake. 


Ndime ya 14: “Iwowa adzamenyana ndi Mwanawankhosa, koma pakuti iye ndiye Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu, Mwanawankhosayo adzawagonjetsa. Komanso oitanidwa aja, amene ali osankhidwa mwapadera ndi okhulupirika, nawonso adzagonjetsa naye limodzi.”

Ngakhale kuti Satana adzafuna kumenya nkhondo ndi Yesu Khristu, iye sadzakwanira kwa Iye. Oyera, naonso, adzamugonjetsa iye mukumenyana kwao ndi iye. Ambuye adzapatsa oyera mphamvu kuti amenyane ndi kumupambana Wosusa Khristu mwa chikhulupiliro chao. Choncho, oyera sadzaopa kumenyana kwao ndi Wosusa Khristu, koma adzakhala mnthawi zomaliza mmtendere ndiponso odekha mtima pokhulupilira mwa Ambuy e Mulungu wawo. Ndiyeno iwo adzapambana adani awo ndi chikhulupiliro chao mwa Ambuye. 

Kupambanaku kwa oyera kutanthauza kuti iwo adzateteza chikhulupiliro chao ndipo adzaphedwa. Ngati nthawiyi yabwera, oyera adzagonjitsa Satana ndiponso Wosusa Khristu polara kuphedwa ndi chikkhulupiliro chao mwa Yesu Khristu ndi chiyembekezo chao cha Ufumu wa Kumwamba, adzatengako mbali mchiukitso ndiponso mkukwatulidwa kwao, adzalandira Ufumu wa tsopano wa Khristu, ndipo zitapita izi adzakhala kwa muyaya mu ulemerero. 


Ndime ya 15: Kenako mngeloyo anandiuza kuti: “Madzi amene wawaona aja, pamene hule lija lakhala, akuimira mitundu ya anthu, makamu, mayiko, ndi zinenero.”

Zipembezo za dziko lapansi zasocheretsa ndipo zalamulira pa anthu a dziko lapansi a mitundu yonse ndi ziphunzitso zake za Satana. Ndimeyi imatiuza kuti ziphunzitso zausatana zogwira nchito pakati pa zipembezo za dziko lapansi zalowa mu mitundu yonse ndi zinenero zonse za dziko lapansi, ndiponso mphamvu yake yafika paukulu kwambiri kotero kuti ibweretse chionongeko ku miyoyo ya anthu. 


Ndime ya 16: “Nyanga 10 waziona zija, komanso chilombo, zimenezi zidzadana nalo hulelo. e Zidzalisakaza ndi kulisiya lamaliseche. Zidzadya minofu yake ndi kulinyeketsa ndi moto.”

Ndime apa imatiuza kuti mitundu ya dziko lapansi idzagwirizana ndi Wosusa Khristu kuti iphe ndi kuononga anthu ake a zipembezo, imatiuza kuti, mmawu ena, kuti anthu a mdzikoli lapansi ndi Wosusa Khristu adzadana ndipo adzachita chiwembu anthu a zipembezo, ndipo adzachotsa zipembezo zina zilizonse za mdziko lapansi kuchoka pa malo ake. Ngakhale kuti anthu a zipembezo a dziko lapansi anapha oyera poyamba mokhalilidwa kumbuyo ndi Wosusa Khristu, iwo okha tsopano adzaonongedwa ndi Satana ndiponso ndi anthu wamba. Satana, pothera, atagwiritsa nchito zipembezo za dziko lapansi kungozikwezeka iyeyekha ngati. 


Ndime ya 17: “Pakuti Mulungu anaika izi m’mitima yawo kuti zichite monga mwa maganizo ake, g kuti zikwaniritse maganizo awo amodzi, mwa kupereka ufumu wawo kwa chilombo, kufikira mawu a Mulungu atakwaniritsidwa.”

Ichi chimatiuza kuti anthu a mdzikoli lapansi adzapereka ufumu wawo ndi mphamvu zawo kwa Satana. Choncho, adzakhala anthu a Wosusa Khristu monga mmene iwo alandira chidzindikiro chake mozipereka, adzamvera bwino kukhala atumiki ake, ndiponso kupha onse amene akukana kulandira chidzindikiro chake. Chotero, kudzunzidwa kwao kwa oyera kudzaloredwa chabe kwa nthawi imene Mawu a Mulungu alora. Mnthawiyi imene yaloredwa, Wosusa Khristu adzachotsa zoipa za mmtima wake wonse ndi kususana ndi Mulungu ndiponso ndi oyera Ake. 


Ndime ya 18: “Ndipo mkazi amene unamuonayo akuimira mzinda waukulu umene ukulamulira mafumu a dziko lapansi.”

Mulungu amatiuza apa kuti dzikoli lapansi lidzakhazikitsa malumulo atsopano kuti lilamulire ndiponso lisonkhanitse mafumu ake, ndipo mafumu adziko lapansi adzalamulilidwa mkumangidwa mkati mwa malamulowa atsopano. Mphamvu yaikulu ya dzikoli lapansi idzalamulira pa mafumu onse adziko lapansi, ngati ndi kuti zinali munthu izo zokha. Dziko lapansi, mmawu ena, lidzapanga malamulo amene adzamangirira mafumu onse pamodzi, ndipo lidzakhala ngati mulungu olamulira pa iwo. 

“Mzinda waukulu” uimilira bungwe la zandale kupyolera mu limene Wosusa Khristu adzalamulilira. Wina aliyense wa dzikoli lapansi adzathera potumikira mgwirizano olamulira dziko lapansi, limene Mulungu anawapatsa iwo, ngati kuti anali Mulungu Iyeyekha, ndipo adzalamulilidwa ndi ilo. Cifukwa anthu adzakhala atumiki a Satana, iwo choncho adzaonongedwa. 

Masalimo 49:20 amatiuza kuti, “Munthu, ngakhale atakhala wolemekezeka, koma ngati ali wosazindikira, Amangofanana ndi nyama zimene zaphedwa.” Choncho, anthu a dzikoli lapansi ayenera kudziwa nthawi isanafike zimene ndi njira za Satana, tsopano khulupilirani mu uthenga wa madzi ndi Mzimu olalikidwa ndi oyera a nthawi ino, ndipo kuchoka pamenepo thawani kuchoka ku tembelero losanduka atumiki a Satana ndipo mmalo mwake khalani obvala dalitso la Ufumu osatha wa Mulungu.