Sermons

[17-2] < Chivumbulutso 17:1-8 > Tiike Nzelu Zathu Pa Chifuniro Chake< Chivumbulutso 17:1-8 >


Chivumbulutso 17:1-5 ikuti, “Mmodzi wa angelo 7 amene anali ndi mbale 7 aja, anabwera n’kundiuza kuti: “Bwera, ndikuonetsa chiweruzo cha hule lalikuluh lokhala pamadzi ambiri, limene mafumu a dziko lapansi anachita nalo dama, ndipo linaledzeretsa anthu okhala padziko lapansi ndi vinyo wa dama lake.” Mu mphamvu ya mzimu, mngeloyo ananditengera kuchipululu. Ndipo ndinaona mkazi atakhala pachilombo chofiira kwambiri, chodzaza ndi mayina onyoza Mulungu. Chinali ndi mitu 7, ndi nyanga 10. Mkaziyo anavala zovala zofiirira ndi zofiira kwambiri. Anadzikongoletsa ndi golide, ndi mwala wina wake wamtengo wapatali, ndiponso ngale. M’dzanja lake, anali ndi kapu yagolide yodzaza ndi zonyansa ndi zinthu zodetsedwa zokhudzana ndi dama lake. Pamphumi pake panalembedwa dzina lachinsinsi lakuti: 

“BABULO WAMKULU, MAYI WA MAHULE NDI WA ZONYANSA ZA PADZIKO LAPANSI.”

Hule mndime ya pamwambapa liimilira zipembezo za padzikoli lapansi, ndipo limatiuza kuti lalowa muzotsekemera limodzi ndi zinthu za dziko lapansi ndi unyinji wa katundu opatsidwa ndi Ambuye. Iwo azikongoletsa iwo okha ndi mtundu uliwonse wa zokongoletsa, ndi ngale za golide ndiponso mphete za diyamondi, ndiponso kuzora mtundu uliwonse wa mafuta onunkhira. Ndime imatiuza kuti zanja lake munali kapu wa golide, ndipo kuti inali yodzaza ndi zonyansa ndi zodetsa za dama lake. Izi ndi zimene Mulungu anaonetsa Yohane. 

Zimene ndimeyi imatiuza ndi kuti Satana akupanga njira mu miyoyo ya anthu ndi kufuna funa kuti iwo azipereke kwa iye powaledzeretsa ndi zinthu za dziko lapansi. mafumu onse a dziko lapansi, naonso, analedzeletsedwa ndi zinthu za dziko lapansi ndi Satana. Choncho, wina aliyense mdzikoli lapansi amaledzeretsedwa ndi vinyo wa dama la dziko lapansi. 

Satana amakwanilitsa zolinga zake ngati anthu aledzeretsedwa ndi zinthu za dziko lapansi, zotsekeretsa zake, ndiponso umbombo wa katundu. Choonadi ndi chakuti cholinga chake ndi chakuti aphimbe anthu kuti asayangane kwa Mulungu. Kuti achite tero, Satana amapanga miyoyo yawo kuti iledzere ndi zinthu za dziko lapansi. tiyenera kuchidzindikira choonadichi. 

Kulibe wina aliyennse mdzikoli lapansi amene sangagwere mmsampha wa katundu. Aliyense amagwera mu za katundu. Zinthu zokongoletsa za dziko lapansi zonse ndi zopangidwa ndiponso zotsogoleledwa ndi Satana. Wina aliyense amaganiza kuti iye ali ndi mabvalidwe a paokha. Koma kumbuyo kwake kuli wozipanga, ndipo wozipangayu ndi wotchedwa Satana. Ichi ndicho cifukwa si tiyenera kukhala onana ndi za katundu, koma mmalo mwake tikhale oledzera ndi Mawu ndiponso ogwira nchito za Mulungu. 

Mawu a Chivumbulutso amene Mulungu analankhula kupyolera mu Mtumwi Yohane ndi chioonadi. Kodi, ndiyeno, nciani cimene Mulungu afuna kutiuza ndi Mawuwa? Ambuye athu amatiuza kuti ife sitiyenera kuzinanitsa tokha ndi dzikoli lapansi, koma mmalo mwake tisusane ndi ilo. Iye amatiuza ife, oyera, mmawu ena, kuti tiganizirepo ndiponso tikhulupilire mwa Mulungu ndi mitima yathu yonse. 

1 Yohane 2:15 ikuti, “Musamakonde dziko kapena zinthu za m’dziko. Ngati wina akukonda dziko, ndiye kuti sakonda Atate.” Ngati mitima yathu ikukonda zinthu za katundu wa dziko lapansi, Mulungu sangakhale mmitima yathu. Koma ngati mitima yathu ikutaila kutali zinthu za dziko lapansi, Mulungu ndiyeno angakhale mmitima yathu. Sitiyenera kukhala miyoyo yathu yonana ndi zinthu za dziko lapansi. Ndipokhapo ngati talingalira pa Mawu a Ambuye athu ndi pa zolinga Zake ndipamene tingatsogoleledwa ndi utsogoleri Wake. 

Tingasinthe malingaliro athu pa nthawi ina iliyonse. Ngati zinthu za dziko lapansi zikufuna kulowa mmitima yathu, nthawi zonse tiyenera kuzikana. Ndipamene tingachotse zinthu zodetsa zonse za dziko lapansi kuchoka mmitima yathu, ndipo mitima yathu mwamsanga imalowa mmtima wa Ambuye. Kodi ndi nciani cymene Ambuye athu amafuna kuchokera kwa ife? Ndipo kodi nciani cimene Iye amatiuza kuti tichite? Kuonetsetsa kuti maganizo otero a umulungu akusefukira mmitima yathu, tiyenera kufafaniza zinthu za dziko lapansi kuchoka ku mitima yathu. 

Mulungu anatipatsa madalitso ambiri, ndipo tsopano tikudzindikira kuti tiyenera kulalikira uthenga wa madzi ndi Mzimu mdziko lonse lapansi kwa matsiku athu onse osala. Choncho ife sitiyenera kumutsitsa otiteteza wathu, ndi kubwera kudzaika nzeru zathu zonse pa chifuniro Chake. Poganizira za nchito zathu za uzimu, tingachotsera kunja zinthu zonse za dziko lapansi zimene zipezeka mmitima yathu. 

Ife oyera tiyenera kuchotsera kunja zinthu za dziko lapansi. Mpaka Ambuye abwerenso, tiyenera kukhala miyoyo yathu ya Chikristu mwa chikhulupiliro. Kukhala chikumbutso cha miyoyo yathu, tiyenera kuchita cimene Ambuye anatipatsa mpaka tikaime pamaso pa Iye. Ndipo tiyenera kukonda Ambuye, ndi kukhala mwa chikhulupiliro, kuchita nchito zilizonse zimene Iye amatilora kuti tichite.