Sermons

[18-1] < Chivumbulutso 18:1-24 > Dziko la Babulo Lagwa< Chivumbulutso 18:1-24 >

“Zimenezi zitatha, ndinaona mngelo wina akutsika kumwamba wokhala ndi ulamuliro waukulu. Ndipo dziko lapansi linawala ndi ulemerero wake. Iye anafuula ndi mawu amphamvu, akuti: ‘Wagwa Babulo Wamkulu wagwa, ndipo wakhala malo okhala ziwanda, ndiponso obisalamo mpweya uliwonse wonyansa wotuluka m’kamwa, komanso obisalamo mbalame iliyonseyonyansa ndi yodedwa. Iye wamwetsa mitundu yonse ya Anthu vinyo wa mkwiyo, vinyo wa dama lake. Ndipo mafumu a dziko lapansi anachita naye dama. Amalonda oyendayenda a padziko lapansi analemera chifukwa cha zinthu zambiri zamtengo wapatali zimene mkazi ameneyu anadziunjikira mopanda manyazi.’ Ndipo ndinamva mawu ena kumwamba, akuti: ‘Tulukani mwa iye anthu anga, ngati simukufuna kugawana naye machimo ake, ndiponso ngati simukufuna kulandira nawo ina ya miliri yake. Pakuti machimo ake aunjikana mpaka kumwamba, ndipo Mulungu wakumbukirad zochita zake zopanda chilungamo. M’bwezereni monga mmene iye anachitira. M’chitireni mowirikiza kawiri. Ndithu, wirikizani kawiri zinthu zimene iyeyo anachita. M’kapu imene anaikamo chakumwa chosakaniza, ikanimo chakumwa chakecho kuwirikiza kawiri. Pa muyezo umene anadzipezera ulemerero ndi kusangalala ndi chuma mopanda manyazi, pa muyezo womwewo mumuzunze ndi kumuliritsa. Pakuti mumtima mwake akumanena kuti, ‘Ine ndine mfumukazi. Sindine mkazi wamasiye, ndipo sindidzaliram ngakhale pang’ono.’ Ndiye chifukwa chake m’tsiku limodzi, miliri yake idzafika. Miliri yakeyo ndiyo imfa, kulira, ndi njala. Ndipo adzanyekeratu ndi moto chifukwa Yehova Mulungu, amene anamuweruza, ndi wamphamvu. ‘Mafumu a dziko lapansi amene anachita naye dama ndi kusangalala ndi chuma mopanda manyazi, adzalira ndi kudziguguda pachifuwa ndi chisoni chifukwa cha iye, poona utsi wofuka chifukwa cha kupsa kwake. Ndipo ataima patali poona kuzunzika kwake, adzati, ‘Kalanga ine! Kalanga ine! Mzinda waukuluwe! u Babulo iwe, mzinda wamphamvu! Chifukwa mu ola limodzi, chiweruzo chako chafika!’ ‘Komanso, amalonda oyendayenda wa padziko lapansi adzamulira maliro ndi kumva chisoni, chifukwa palibenso wina wowagula katundu wawo yense, katundu yensea wagolide, siliva, mwala wamtengo wapatali, ndi ngale. Komanso palibe wowagula nsalu zabwino kwambiri, zofiirira, zasilika, zofiira kwambiri, ndi mtengo uliwonse wa fungo lokoma, komanso chilichonse chopangidwa ndi mnyanga, chilichonse chopangidwa ndi mtengo wapamwamba, ndi chamkuwa, chachitsulo, ndi chamwala wa mabo. Komanso palibe wowagula sinamoni, amomo, zofukiza, mafuta onunkhira, lubani, vinyo, mafuta a maolivi, ufa wabwino kwambiri, tirigu, ng’ombe, nkhosa, mahatchi, ngolo, akapolo, ndi anthu. Zoonadi, chipatso chabwino chimene moyo wako unali kulakalakad chakuchokera. Zinthu zako zonse zabwino ndi zokongola zawonongeka, ndipo anthu sadzazipezanso. ‘Amalonda oyendayenda a zinthu zimenezi, amene analemerera pa iye, adzaima patali chifukwa cha mantha poona kuzunzika kwake. Iwo adzamulira maliro ndi kumva chisoni ndipo azidzati, ‘Kalanga ine! Kalanga ine! Mzinda waukuluwe wovala zovala zapamwamba, zofiirira, ndi zofiira kwambiri. Mzinda wokongoletsedwa mochititsa kaso iwe, ndi zokongoletsera zagolide, zamwala wamtengo wapatali, ndi zangale. Zachisoni, chifukwa mu ola limodzi, chuma chochulukachi chawonongedwa!’ ‘Woyendetsa ngalawa aliyense ndi munthu aliyense woyenda panyanja kuchokera kulikonse, k ogwira ntchito m’ngalawa ndi onse oyenda pa nyanja pochita malonda awo, anaimapatali. Poona utsi wofuka chifukwa cha kupsa kwake, iwo anafuula kuti, ‘Ndi mzinda uti ungafanane ndi mzinda waukulu umenewu?’ Iwo anathira fumbi pamitu pawo akufuula, kulira ndi kumva chisoni, ndipo anati, ‘Kalanga ine! Kalanga ine! Mzinda waukuluwu, umene unalemeretsa onse okhala ndi ngalawa panyanja chifukwa cha chuma chake chamtengo wapatali, pakuti mu ola limodzi, wawonongedwa.’ ‘Kondwerani kumwambako chifukwa cha zimene zamuchitikira. Inunso oyera, inu atumwi, ndi inu aneneri, kondwerani chifukwaMulungu wamuweruza ndi kumupatsa chilango chifukwa cha zomwe anakuchitirani.’ Ndiyeno mngelo wamphamvu ananyamula mwala waukulu ngati wa mphero n’kuuponya m’nyanja, m ndipo anati: ‘Mzinda waukulu wa Babulo udzaponyedwa pansi mofulumira ndi mwamphamvu chonchi, ndipo sudzapezekanso. Pamenepo kuimba Kwa oimba motsagana ndi zeze, Kwa oimba zitoliro, Kwa oimba malipenga, ndi Kwa oimba ena, sikudzamvekanso mwa iwe. Mwa iwe simudzapezekanso mmisiri wa ntchito iliyonse, ngakhale phokoso la mphero silidzamvekanso mwa iwe. Kuwala kwa nyale sikudzaunikansomwa iwe. Mawu a mkwati ndi a mkwatibwi sadzamvekanso mwa iwe, chifukwa amalonda ako oyendayenda anali anthu apamwamba padziko lapansi, ndiponso mitundu yonse ya anthu inasocheretsedwa ndi zochita zako zamizimu. Mwa iye munapezeka magazi a aneneri, u a oyera,a ndi a onse amene anaphedwa padziko lapansi.’” Kusanthula


Ndime ya 1: Zimenezi zitatha, ndinaona mngelo wina akutsika kumwamba wokhala ndi ulamuliro waukulu. Ndipo dziko lapansi linawala ndi ulemerero wake. 

Kupyolera mu atumiki amene Mulungu anatumiza padzikoli lapansi kuti achite nchito Yake, anthu angamve ziphunzitso za madalisto a Mulungu ndiponso matemberero. Kuti mmasuke kuchoka ku machimo anu onse ndiponso kuchisoni chanu, choncho, onse ainu muyenera kulandira ndiponso kukhulupilira mu Mawu ya madalitso a Kumwamba mmitima yanu olalikidwa ndi atumiki a Mulungu. 


Ndime ya 2: Iye anafuula ndi mawu amphamvu, akuti: “Wagwa Babulo Wamkulu wagwa, ndipo wakhala malo okhala ziwanda, ndiponso obisalamo mpweya uliwonse wonyansa wotuluka m’kamwa, komanso obisalamo mbalame iliyonseyonyansa ndi yodedwad!”

Mmawu akuti “Babulo wamkulu wagwa,” mawu akuti Babulo amagwiritsidwa nchito mu Baibulo kuimilira dziko lamakono. Mu Pangano la Kale, mwachisanzo, timapeza nkhani ya Sanja ya Babelo, Sanja yomangidwa ndi anthu kufunafuna kuti apandukire Mulungu posonkhanitsa pamodzi mphamvu zawo, imene inagwetsedwa ndi Mulungu pa cifukwa cimeneci. Ngati ndime ya pamwamba ikunena kuti Babulo wamkulu wagwa, imatiuza kuti dzikoli lapansi lidzagwa. Kuli anthu ena amene angaganize kuti, “tsopano dzikoli lapansi ndi lolimba bwino bwino, ndipo kodi lingagwenso motani?” koma Mulungu apa amatiuza kuti ngati miliri ya mbale zisanu ndi ziwiri yathiridwa mosatirana wina ndi mzache, Iye adzatsitsa dzikoli lapansi chimodzimodzi ngati ndimmene anagwetsera Sanjay a Babelo. 

Kodi, ndiyeno, cifukwa n’ciani dzikoli lapansi lidzaonongedwa ndi Mulungu ndi miliri ya mbale 7? Ndi cifukwa anthu a dzikoli nlapansi adzagwirizana iwo okha ndi Wosusa Khristu pakupha oyera obadwa-mwatsopano amene akhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu, ndiponso ndi cifukwa chakuti iwo choncho ndimmene adzasunanirana ndi Mulungu mpaka ku mapeto awo. Ndi cifukwanso chakuti dzikoli lidzakhala “malo okhalamo ziwanda.” 

Cifukwa n’ciani uwu ndi umene udzakhala mlandu? Cifukwa n’ciani, cimene, dzikoli lapansi lidzakhala malo okhalamo ziwanda? Ndi cifukwa chakuti ngati nthawi yomaliza yabwera, anthu ambiri adzazipereka ku Wosusa Khristu ndi kusandulidwa mu mtumiki oipayu polandira chidzindikiro cha Satana kuchokera kwa iye. 

Mmalemba, Chinjoka chimagwiritsidwa nchito kuimilira Satana, ndipo ziwanda zimilira atumiki a Chinjoka. Choncho, ngati apa akunena kuti dziko lapansi lakhala malo okhalamo ziwanda, atanthauza kuti Wosusa Khristu, mtumiki wa Chinjoka, adzazaza dziko lonse lapansi. Dziko la nthawi zomaliza lidzakumana ndi nthawi ya masautso aakulu ngati miliri ya mbale 7 yathiridwa pa ilo. Dzikoli lapansi lidzakhala dziko la Chinjoka, ndipo ziwanda zithamanga uku ndi uku ngati dziko ndi lawo. Ndipo dzikoli lapansi lidzagwa mwamsanga msanga, kugwetsedwa ndi miliri yomaliza ya mbale 7 zothiridwa ndi Mulungu. 


Ndime ya 3: “Iye wamwetsa mitundu yonse ya Anthu vinyo wa mkwiyo, vinyo wa dama lake. Ndipo mafumu a dziko lapansi anachita naye dama. s Amalonda oyendayenda a padziko lapansi analemera chifukwa cha zinthu zambiri zamtengo wapatali zimene mkazi ameneyu anadziunjikira mopanda manyazi.” Ndipo ndinamva mawu ena kumwamba, akuti: “Tulukani mwa iye anthu anga, ngati simukufuna kugawana naye machimo ake, ndiponso ngati simukufuna kulandira nawo ina ya miliri yake.”

Monga mmene ndimeyi ikunenera apa, mchoona “mitundu yonse” padziko lapansi yaledzera ndi vinyo wa mkwiyo wa dama la dziko lapansi. mmawu ena, anthu adzikoli lapansi akuganiza za dziko lapansi ngati Mulungu, ndipo akhulupilira momo ndiponso kulisatira motero. Iwo akondetsetsa dziko lapansi koposa Mulungu. Dzikoli lapansi lakhala chiyambi cha uchimo, ndipo anthu ake okhala miyoyo yawo yoledzera ndi uchimo. 

Zolukamo, choncho, ndi kugwa kwa dziko lapansi ndi uchimo. Cifukwa anthu akondetsetsa ndi kusatira dziko ngati Mulungu, Iye adzawaononga ndi chilango Chake cha miliri ya mbale 7. Zamoyo zilizonse za mdzikoli lapansi chidzaonongekwa ndi miliriyi 7 yobweretsedwa ndi Mulungu ndipo kuponyedwa mu gehena. 

Mulungu amatichenja poyera-yera kuti wina aliyense amene tsopano sakhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu wopatsidwa ndi Mulungu adzakumana ndi miliri ya mbale 7 pomaliza. Muyenera kukumbukira kuti ngati inu simkhulupilira mu uthengawu ndi kupiliza kususana ndi Mulungu kosakumbukira chenjezo Lake, si kuti mdzalangidwa ndi miliri ya mbale 7 yokha ai, koma mdzalandiranso chilango chosatha cha gehena. 

Anthu ayenera kudzindikira, choncho, kuti tsopano iwo ayenera kukhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu, kotero kuti athawe kuchoka ku miliri yaikulu ndiponso yoopsa ya Mulungu, ndipo ayenera kubwerera kuchikhulupiliro cha mu uthenga woona wa madzi ndi Mzimu posachedwa mwasanga mmene angathere. 

Ngakhale kuti mafumu ambiri ndiponso ochita malonda a mdziko lapansi asonkhanitsa chuma chachikulu ndi kuchuluka kwa katundu wake, onse adzatha alikufuura, achisoni, alikulira ndiponso kulira mofuura ngati aona dzikoli lapansi likugwa ndi miliri yaikulu yobweretsedwa ndi Mulungu. 

Choncho, tonse si tiyenera kuiwala kuti tiyenera kualalikira uthenga wa madzi ndi Mzimu kwa wina aliyense, ndi kuti tiyenera kukhala miyoyo yathu yoyangana ku zaka chikwi za tsopano. Tiyenera kutsogolera wina aliyense ku uthenga wa madzi ndi Mzimu, kotero kuti munthu aliyense athawe kuchoka ku miliri yaikulu. 


Ndime ya 4: Ndipo ndinamva mawu ena kumwamba, akuti: “Tulukani mwa iye anthu anga, ngati simukufuna kugawana naye machimo ake, ndiponso ngati simukufuna kulandira nawo ina ya miliri yake.”

“Tulukani mwa iye anthu anga, ngati simukufuna kugawana naye machimo ake, ndiponso ngati simukufuna kulandira nawo ina ya miliri yake.” Awa ndi Mawu a Mulungu olankhula ku oyera ake. Oyera sayenera, mmawu ena, kukhala a dziko lapansi la nthawi zomaliza ndi kukhala miyoyo yawo ngati ukapolo wake. Ngakhale onse aja anakhala oyera kale, ngati agwera mu machimo adziko lapansi sadzakwanitsa kupewa kuweruzidwa ndi Mulungu ndi miliri Yake yoopsa. Mulungu auza oyera onse, mmawu ena, kuti asaunjike mkwiyo Wake potsirizira kukhala akapolo adziko lapansi. 


Ndime ya 5: “Pakuti machimo ake aunjikana mpaka kumwamba, ndipo Mulungu wakumbukira zochita zake zopanda chilungamo.”

Mulungu amakumbukiradi machimo onse ndi zochita za dzikoli lapansi ndipo ayembekeza chabe tsiku lachiweruzo chake. Ndi kuonekera mwadzizizi kwa Wosusa Khristu tsiku lina, chionongeko posachedwa chidzabwera padziko lonse monga mmene anakonzera Mulungu. komabe kuli anthu ena amene okhuluplira kuti dzikoli lapansi silidzaonongedwa, koma kuti lidzakhala kwa muyaya. 

Dzikoli, choncho, si lidzakhala mmene iwo aganizira, koma lidzaonongedwa mwadzizizi ndi miliri ya malipenga 7 ndiponso ya mbale 7 yobweretsedwa ndi Mulungu. Ngati nthawi yomaliza yabwera, Mulungu adzabweretsa masautso kulikonse mdziko lapansi ndi kuliononga. Choncho tiyenera kukhala ozipereka mu miyoyo yathu ya chikhulupiliro mpaka kothera kwenikweni, kugwililira njii ku chikhulupiliro chathu kuti Ufumu wa Yesu Khristu udzabweradi. 

Mulungu asanalamulire angelo Ake athire mbale 7 padzikoli lapansi, machimo adziko lapansi adzakhala ochulukirachulukira ndipo adzafalitsidwa konsekonse kwambiri koyenerera kulandira chiweruzo cha Mulungu. Choncho Mulungu adzakumbukira machimo ailo, ndipo sadzagwiliriranso chionongeko chailo. Moonjezera, Wosusa Khristu ndi anthu a zadziko lapansi adzakhala ali kuzunza anthu a Mulungu, kukakamiza oyera kuti akane chikhulupiliro chao, ndiponso kupanga ophedwa pakati pa iwo. Ngati zinthuzi zachitika, dzikoli lapansi lidzakumana ndi miliri ya mbale 7. 


Ndime ya 6: “M’bwezereni monga mmene iye anachitira. M’chitireni mowirikiza kawiri. Ndithu, wirikizani kawiri zinthu zimene iyeyo anachita. M’kapu imene anaikamo chakumwa chosakaniza, ikanimo chakumwa chakecho kuwirikiza kawiri.”

N’cholembedwa apa kuti, “M’bwezereni monga mmene iye anachitira.” Ichi chiimilira dzikoli lapansi, otchedwa ochimwa okhala mmenemo, Wosusa Khristu, ndi Satana. Imatiuza kuti Mulungu adzabwezera monga mmene anabweretsera mazunzo, kupweteka, chisautso ndiponso imfa pa oyera. 

Ndime ya 6 ikunenanso kuti, “m’kapu imene anaikamo chakumwa chosakaniza, ikanimo chakumwa chakecho kuwirikiza kawiri.” Uku ndi kulamulo kwa Mulungu kopatsidwa kwa angelo Ake kuti alange zipembezo zachinyengo zonse za dziko lapansi zimene zatsogolera anthu ku gehena pofalitsa maboza a Mdyerekezi. Chitanthauza kuti Mulungu adzabweretsa mkwiyo Wake ndiponso chilango pa Chikristu cha matsiku ano cifukwa cha uchimo wake cha kupereka ziphunzitso za chinyengo, kusakaniza Mawu a Mulungu ndi ziphunzitso za Satana, ndipo kuchoka pamenepo kutsogolera anthu kwa Mdyerekezi. Choncho, Akristu amene sakhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu adzalandira chilango chimodzimodzi cha uchimo ngati anthu wamba za dziko lapansi. 


Ndime ya 7: “Pa muyezo umene anadzipezera ulemerero ndi kusangalala ndi chuma mopanda manyazi, pa muyezo womwewo mumuzunze ndi kumuliritsa. Pakuti mumtima mwake akumanena kuti, ‘Ine ndine mfumukazi. Sindine mkazi wamasiye, ndipo sindidzaliram ngakhale pang’ono.’” 

Apa Mulungu moyankha akuti machimo a anthuwa ozitukumula ndi kupwetekedwa ndiponso achisoni. Ku anthu onse a zipembezo za dziko lapansi amene sanabadwe mwatsopano, ndiponso ku onse osakhulupilira, anthu nwamba a dziko lapansi, Mulungu adzakumbutsa machimo awo ndi kuwalanga. 

Komabe adzakhala ozitukumula kwambiri, n’kunena kwa iwo okha, “Ine ndine mfumukazi. Sindine mkazi wamasiye, ndipo sindidzalira ngakhale pang’ono.” Choncho Mulungu adzabweretsa kwa iwo miliri ya chionongeko chao. Ndi miliri yaikulu yobweretsedwa ndi Mulungu, onse adzazunzidwa ndi chisoni chakutaya zinthu zonsi zimene anali nazo za padziko lapansi ndi okondedwa awo, zonse pa nthawi imodzi. 


Ndime ya 8: “Ndiye chifukwa chake m’tsiku limodzi, miliri yake idzafika. Miliri yakeyo ndiyo imfa, kulira, ndi njala. Ndipo adzanyekeratu ndi moto chifukwa Yehova Mulungu, amene anamuweruza, ndi wamphamvu.” 

Ndi kuyamba kwa miliri 7, miliri ya imfa, yolira ndiponso ya njala idzabwera padzikoli lapansi mu tsiku limodzi. Wosusa Khristu ndi omsatira ake a dziko lapansi choncho ndimmene adzalangidwira kuotcha kwa muyaya mgehena. 


Ndime ya 9: “Mafumu a dziko lapansi amene anachita naye dama ndi kusangalala ndi chuma mopanda manyazi, adzalira ndi kudziguguda pachifuwa ndi chisoni chifukwa cha iye, r poona utsi wofuka chifukwa cha kupsa kwake,”

Anthu ndiponso mafumu adziko lapansi adzachitira umboni ndi maso awoawo dziko lawo ligolera moto ndi zivomezi ndiponso kuonongedwa ndi miliri ya mbale 7. Mafumu adziko lapansi choncho adzalira ndiponso adzafuura, adzalira mofuura cifukwa cha kutaya kwao. 


Ndime ya 10: “Ndipo ataima patali poona kuzunzika kwake, adzati, ‘Kalanga ine! Kalanga ine! Mzinda waukuluwe! u Babulo iwe, mzinda wamphamvu! Chifukwa mu ola limodzi, chiweruzo chako chafika!’”

Anthu amene sanakhulupilire kuti dzikoli lapansi lidzagwa lidzakhuzidwa ndi mantha ngati awo dziko lose likugwadi pomwe alikupenya ndi maso awo. Padziko limene likuwala kwambiri cifukwa chokongora kwake, chiweruzo cha Mulungu chadzatsika tsiku ndi limodzi, ndipo chidzagwa chonse kamodzi kokha chabe. 


Ndime ya 11-13: “Chifukwa mu ola limodzi, chiweruzo chako chafika!” “Komanso, amalonda oyendayenda wa padziko lapansi adzamulira maliro ndi kumva chisoni, chifukwa palibenso wina wowagula katundu wawo yense, katundu yensea wagolide, siliva, mwala wamtengo wapatali, ndi ngale. Komanso palibe wowagula nsalu zabwino kwambiri, zofiirira, zasilika, zofiira kwambiri, ndi mtengo uliwonse wa fungo lokoma, komanso chilichonse chopangidwa ndi mnyanga, chilichonse chopangidwa ndi mtengo wapamwamba, ndi chamkuwa, chachitsulo, ndi chamwala wa mabo. Komanso palibe wowagula sinamoni, amomo, zofukiza, mafuta onunkhira, lubani, vinyo, mafuta a maolivi, ufa wabwino kwambiri, tirigu, ng’ombe, nkhosa, mahatchi, ngolo, akapolo, ndi anthu.”

Kodi ndani amene adzagula kapena kugulitsa kanthu kulikonse ngati chionongeko cha dziko lapansi chayandikira? Ochita za malonda pa dzikoli lapansi, naonso, adzalira ndi kufuura cifukwa chakataya dziko lawo lapansi. ngati Mulungu athira miliri ya mbale 7, kulibe wina aliyense mdziko lapansi adzakahala ali kugura kanthu kena kulikonse. Ichi sichidzapangidwanso, ndipo ndi Ufumu wa Yesu Khristu okha umene udzamangidwa pa chionongeko chake. 

Uwu apa ndi mundandanda wa ochita malonda oyenayenda umene anthu amazikongoletsa okha ndi zinthu za pamwamba mpaka tsiku lelo. Koma zonse zithunzi zidzakhala zopanda phindu mtsiku limodzi chabe, ndipo kulibe wina aliyense amene adzafunanso zinthu zotero za dziko lapansi. zonse zinthuzi ndi zimene zipembezo za dziko lapansi zimabweretsa. Zipembezo za dziko lapansi zichita zinthu zonse mothekera cifukwa cha chikondi cha chuma, kosakhala ndi mantha ngakhalenso kugulitsa miyoyo ndi peni imodzi.


Ndime ya 14-18: “Zoonadi, chipatso chabwino chimene moyo wako unali kulakalakad chakuchokera. Zinthu zako zonse zabwino ndi zokongola zawonongeka, ndipo anthu sadzazipezanso. Amalonda oyendayenda a zinthu zimenezi, amene analemerera pa iye, adzaima patali chifukwa cha mantha poona kuzunzika kwake. Iwo adzamulira maliro ndi kumva chisoni 16 ndipo azidzati, ‘Kalanga ine! Kalanga ine! Mzinda waukuluwe wovala zovala zapamwamba, zofiirira, ndi zofiira kwambiri. Mzinda wokongoletsedwa mochititsa kaso iwe, ndi zokongoletsera zagolide, zamwala wamtengo wapatali, ndi zangale. Zachisoni, chifukwa mu ola limodzi, chuma chochulukachi chawonongedwa!’ Woyendetsa ngalawa aliyense ndi munthu aliyense woyenda panyanja kuchokera kulikonse, ogwira ntchito m’ngalawa ndi onse oyenda pa nyanja pochita malonda awo, anaimapatali. Poona utsi wofuka chifukwa cha kupsa kwake, iwo anafuula kuti, ‘Ndi mzinda ?’”

Choncho anthu sadzakwanitsanso kuona katundu wa dziko lapansi. 

Ochita malonda amene analemera kupyolera mu mdzikoli lapansi adzalira ndi kuufura ngati aona dziko lawo lapansi likugwa. Adzalira mofuura mokuda nkhawa, cifukwa ngati dziko lagwa, iwo, naonso, adzagwa nalo limodzi, ndipo unyinji wonse wa chuma chao udzazimiririka mtsiku limodzi lokha.

Ngati zipembezo zomangidwa mchuma cha dziko lapansi, anthu adzikoli adzazipeza okha alikulira mofuura iwo okha, “mawe, mawe!” Ochita malonda a ku maiko akutali ndiponso ena angalawa zotawutsira makatundu kudziko lina naonso adzalira mofuura. Anthuwa adzalira mokuda nkhawa, “Kodi n’chitukuko chotani chinamangidwapo ndi anthu chinakhala chachikulu ndipo chabwino koposa cha matsiku ano?”


Ndime ya 19: “Iwo anathira fumbi pamitu pawo akufuula, kulira ndi kumva chisoni, d ndipo anati, ‘Kalanga ine! Kalanga ine! Mzinda waukuluwu, umene unalemeretsa onse okhala ndi ngalawa panyanja chifukwa cha chuma chake chamtengo wapatali, pakuti mu ola limodzi, wawonongedwa.’” 

Kuona dziko lapansi ligwetsedwa pansi ndi miliri ya mbale 7, onse amene anali kuganiza kuti dzikoli lapansi lidzakhala kwa muyaya adzakhala alikuilra mchisoni chachikulu. Onse amene okhalabe mdzikoli lapansi adzakhala alikulira ndi kufuura pamene alikuchitira umboni dziko lonse likuonongedwa kamodzi kokha ndi miliri ya mbale 7 yobweretsedwa ndi Mulungu, koma kulira kwao konse kudzakhala kopanda nchito, cifukwa pa nthawi yomweyo ndiyeno dzikoli lapansi ndiponso zinthu zonse mmenemo zitantha kale. Ngati ali ndi mphamvu zolira ndiyeno, ayenera kulira tsopano pa zotulukamo zawo, kuti iwo ndi ogamulidwa ku gehena cifukwa cha machimo awo, ndipo ayenera kukhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu kuti aomboledwa kuchoka kuchionongeko chao chosatha. 


Ndime ya 20: “Kondwerani kumwambako chifukwa cha zimene zamuchitikira. Inunso oyera, inu atumwi, ndi inu aneneri, kondwerani chifukwaMulungu wamuweruza ndi kumupatsa chilango chifukwa cha zomwe anakuchitirani!”

Oyera okwatulidwa mmtambo adzakondwera ngati miliri ya mbale 7 yabweretsedwa, cifukwa ndi miliriyi Mulungu adzabwezera iwo onse. Ndichoyenera kuti Mulungu choncho athire yoopsa, miliri yaikulu pa adani Ake. 

Ndime ya 21: Ndiyeno mngelo wamphamvu ananyamula mwala waukulu ngati wa mphero n’kuuponya m’nyanja, m ndipo anati: “Mzinda waukulu wa Babulo udzaponyedwa pansi mofulumira ndi mwamphamvu chonchi, ndipo sudzapezekanso.”

Apa Mulungu akuti dzikoli silidzaonekanso, monga mmene mwala olema uponyedwa mnyanja. Ambuye athu ndiyeno adzapanganso dziko la tsopano ndiponso zinthu zonse mmenemo, ndi kukwanilitsa nchito Yake yosandutsa dziko lapansi kukhala Ufumu wa Khristu. 


Ndime ya 22: “Pamenepo kuimba kwa oimba motsagana ndi zeze, kwa oimba zitoliro, kwa oimba malipenga, ndi kwa oimba ena, sikudzamvekanso mwa iwe. Mwa iwe simudzapezekanso mmisiri wa ntchito iliyonse, ngakhale phokoso la mphero silidzamvekanso mwa iwe.”

Ngati miliri ya mbale 7, kulibe kuimba kulikonse kumene anthu anamvapo mdzikoli lapansi kumene kudzamvekanso, kapena phokosa la kumenya zibeketa za okhoma zibeketi kudzamveka. 


Ndime ya 23: “Kuwala kwa nyale sikudzaunikansomwa iwe. Mawu a mkwati ndi a mkwatibwi sadzamvekanso mwa iwe, chifukwa amalonda ako oyendayenda anali anthu apamwamba padziko lapansi, ndiponso mitundu yonse ya anthu inasocheretsedwa ndi zochita zako zamizimu.”

Ngati miliri ya mbale 7 yakwanilitsidwa, dzikoli lapansi silidzaonanso kuwala kwa nyale, kapena kumvanso. Chinyengo cha cha wa mayele nachonso chidzatha, cifukwa dziko ndyeno lidzatha. 


Ndime ya 24: “Mwa iye munapezeka magazi a aneneri, u a oyera, a ndi a onse amene anaphedwa padziko lapansi.” 

Cifukwa cimene Mulungu adzathirira miliri yaikulu ya mbale 7 padzikoli lapansi ndi cifukwa chakuti atumiki a Satana adzakhetsa magazi a anneneri ndi oyera Ake.