Sermons

[18-2] < Chivumbulutso 18:1-24 > “Tulukani mwa Iye, Anthu Anga, Ngati Simukufuna Kulandira Nawo Ina Ya Miliri Yake”< Chivumbulutso 18:1-24 >


Mulungu mu chapitala 18 amatiuza kuti Iye adzaononga mzinda wamkulu Babulo ndi miliri Yake. Cifukwa kufika pa nthawi yomaliza dzikoli likanasanduka lonyansa kwambiri ndiponso la uchimo pamaso pa Mulungu, ndipo cifukwa Mulungu chotero sadzakhalanso ndi funiro lina koma kuliononga ngakhale kuti analilenga Iyeyekha, Iye adzalora miliri yaikulu, imene idzatsiriza dziko lapansi. Dzikoli lidzaonongedwe mpaka litheretu.

Cifukwa chenicheni cymene Mulungu adzaongera dziko ndi cifukwa Iye adzaona magazi a aneneri ndi oyera Ake. Ndiponso cifukwa dzikoli lachita machimo ambiri ndiponso aakulu kwambiri ndi zinthu zonse zimene Mulungu analipatsa, linakakhala lonyansa kwambiri kotero kuti Mulungu alilore. Dziko lokongola kwambiri limene Mulungu analenga ndi dziko lapansi. Ichi ndi cifukwa chakuti Mulungu Iyeyekha anagwirira nchito padzikoli lapansi ndi chidwi mofunikira, ndiponso n’cifukwa chakuti ndi malo amene zolinga ndi nchito ya Mulungu yopulumutsa ochimwa mwa Yesu Khristu inakwanilitsidwira. 

Ngakhale chonchi, Mulungu anakonza kale mmene Iye adzaonongera dzikoli ndi mmene adzapangira Ufumu wa Yesu Khristu kubwera. Ngati dzikoli lidzaza ndi mtundu uliwonse wa zonyansa, Mulungu adzaliononga kupyolera mwa angelo Ake ndi miliri ya mbale 7. Iye ndiyeno adzapanganso zinthu zonse kukhala za tsopano ndi kulora oyera Ake kulamulira m dziko Lake la tsopano. Mzinda Wa Kugwa Wa Babulo!


Mafumu adziko lapansi achita dama ndi zinthu za dziko ndi kukhala mzapamwamba zake, pamene ochita malonda, naonso atangwanidwa ndi kugulitsa ndi kugura zinthu zonse zimene Mulungu anawapatsa, amutaya Mulungu Iyeyekha cifukwa chofunitsitsa kwa umbombo. Mulungu adzaononga zinthu zonse ndiponso zomanga—zonse, zipembezo, malonda opezeka mkati mwa zipembezo, anthu amene adzailemeletsa iwo okha kupyolera mu zipembezo, mafumu, azandale, anthu odzaza ndi mtima ofunitsitsa kukhala ndi chuma, ndi ena ambiri—onsewa adzatsitsidwa ndi Mulungu. 

Mulungu adzagwatsa zomanga zina zilizonse padzikoli lapansi ndipo sadzatsiyako chomanga china chilichonse choimilire, ndipo Iye adzaonga zinthu zonse, kuchoka ku anthu mpaka ku maudzu ndi ku mitengo, ndi moto Wake. Ngati zinthu zonse mdzikoli zagwa chonchi, anthu adzaliira maliro ndi kufuura. Makamaka, Mulungu adzaonetsetsa kuti aononga onse amene azilemeletsa okha kupyolera mu zipembezo. Ndichofunikira kwambiri kuti ife tidziwe nthawi isanafike ndi kukhulupilira mchoona kuti Mulungu ndimmene adzaonongera dzikoli lokongola limene Iye analenga Iyeyekha. 

Pa nthawiyi, Mulungu adzalora oyera obadwa-mwatsopano amene anatengako mbali mchiukitso choyamba cha Yesu Khristu kuti alamulire padzikoli lapansi kwa zaka chikwi chimodzi. Ndi Ufumu wa Ambuye, Iye adzabwezera oyera cifukwa chotumikira uthenga wa madzi ndi Mzimu ndiponso cifukwa cha kuphedwa kuti ateteze chikhulupiliro chao pamene anali padzikoli lapansi. Mulungu adzawapatsa ulamuliro pa mizinda 10, ndiponso pa mizinda isanu, ndiponso pa mizinda iwiri ndi kuwalora kuti alamulire kwa zaka chikwi chimodzi, ndipo chitatha ichi, Iye adzawapatsanso Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi kuti akhale muyaya. 

Cifukwa n’ciani, cimene, Mulungu adzaonongera dziko lapansi, dziko lokongola kwambiri mdziko lonse? Ndi mdzikoli lapansi lokha mmene nsomba zingasambire mmitsenje, nyama zamnkhalango zingaziyendayenda msanga, ndiponso anthu angakhale momo. Koma cifukwa Mulungu sadzakwanitsa kuloranso dziko mmene uchimo wafalikira kwambiri, Iye adzaika dzikoli muchionongeko chotherathu ndi miliri Yake. Mulungu anakonza kuononga dziko. 

Wina aliyense okhala padzikoli lapansi, kuchotsako amene anapulumutsidwa, adzaonongedwa ndi miliri ya mbale 7. Cifukwa olungama onse a mnthawi zomaliza adzaphedwa, adzazunzidwa ndi kupondelezedwa ndi dzikoli lapansi, Mulungu adzaponda padziko ilo limene mobwezera zochita zake zoipa. Ngati nthawiyi yabwera, atsogoleri azipembezo ndi ochita malonda amene amene anali kuchita malonda mwa miyoyo za anthu onse adzaonongedwa. Mulungu sadzapha kokha onse amene anali kukhala ngati azitsogoleri a zipembezo kopanda kubwadwa mwatsopano, komanso Iye adzawaponya, limodzi ndi Mdyerekezi, mung’anjo ya moto ndi sulufure. 

Mulungu adzaongadi dzikoli. Choncho, timadzindikira kwambiri ndi kukhulupilira mopitilira malire a kukaikira kuti dziko lidzaonongedwa. Mulungu adzapha onse ochita malonda amene amazitukumula ndi mitundu yonse ya zinthu zazikulu ndi kuyendayenda mu miyoyo ya anthu ndi zipembezo zawo. Ndipo komabe, ngakhale kuti miliri ya Mulungu ili pafupi, anthu okhalabe mukuzitukumula kwao mchiyembekezo chao. Mngopenya chabe pa azitsogoleri a zipembezo a dzikoli lapansi. Sikuti onse ndi ozitukumula, ngati alikuchita zinthu zoyenera pamaso pa Mulungu? Kodi Mulungu adzaloradi zimene anthu otero alikuchita? 

Ngati Mulungu anati Iye adzaononga dzikoli lapansi cifukwa cha machismo ya anthuwa, ndiyeno tiyenera kukhulupilira motero, cifukwa zinthu zonse zidzachitika kulingana ndimmene Mulungu analankhulira kuti zidzachitika. Ndipo tiyenera kuteteza chikhulupiliro chathu. Sindinena ichi ngati wina wache wa amodzi azitsogoleri amene apanga ziphunzitso zawo zazing’ono zachipembezo ndi kulankhula pa zakubwera kwa apocalypse, koma Ndinena ichi cifukwa tiyenera kukhulupilira mu zimene Mulungu anatiuza mu Malemba—cimene ndi, Mulungu Wamoyo adzaonongadi dzikoli ndi miliri yaikulu ya mbale 7. Tisalowe Ife Tokha mdziko lapansi limene Posachedwapa Lidzaonongedwa 


Choncho, tisatengedwe ndi kuziunjikira chuma cha dzikoli limene posachedwapa lidzaonongedwa. Tiyenera kukhutira ndi zimene Mulungu atipatsa, ndi kuzidwiritsa nchito ndiponso kugawana mmene Mulungu amafunira. Zinthu za mkatundu wa dziko lapansi zimafunika potumikira Mulungu pokha. Tiyenera kukhala ngati mtumiki okhulupirika wa Mulungu amene amasamalira zimene Mulungu amupatsa cifukwa chakulalikira uthenga. Tisakokedwe ndi zinthu za katundu za mdziko lapansi, pakuti timakhulupilira kuti Mulungu adzaononga dzikoli lapansi. 

Tisaziputsitse tokha poganiza kuti chuma ndi kulemera kwa dzikoli lapansi kudzakhala kwa muyaya. Podziwa kuti Mulungu adzaponda pa atsogoleri azipembezo onse ndi owasatira awo limodzi, tiyenera kukhala oyembekezera tsiku la kubweranso kwa Ambuye. Ngati sititero, tidzathera pogwera mdziko lapansi, dziko limene posachedwa lidzaonongedwa. Choncho, kuti tisagwere mdziko limene lidzakumana ndi chionongeko chake, tiyenera kukhulupilira kuti dziko lapansi lidzaongedwadi. 

Mulungu alimoyo pa nthawi yomweyi, ndipo ngati nthawi yabwera, Iye adzakwanilitsa zonse zimene Iye analankhula. Pamene chili choona kuti ngakhale pakati pa obadwa-mwatsopano pali ena amene chikhulupiliro chao kufikira tsopano chisanakure, choncho tonse tiyenera kukhulupilira kosakaika. Ndipo tonse tiyenera kuukanso. Tisataye mitima yathu kudziko lapansi limene posachedwa lidzaonongedwa, koma mmalo mwake tikhale miyoyo yathu poika chikhulupiliro chathu chosatopa ndiponso chosagwendezeka mu Mawu a Mulungu. mitima yathu tingafooke nthawi zina, koma tiyenerabe kukhala ndi chikhulupiliro cholimba. 

Kunena kuti Mulungu adzachita nchito zonsezi padzikoli lapansi ndi chinthu chokoma kwa ife. Kukanakhala kuti Mulungu sadzaononga dzikoli lapansi ndi kumanganso Ufumu wa tsopano wa Khristu mmalo ake, olungama akanakhala okhumudwa kwakukulu. Ichi ndicho cifukwa cholinga cha Mulungu ndichokoma, ndipo ndi cifukwa chake Iye amaperekera chiyembekezo ku oyera olungama. 

Ngati osakhulupilira akanakhalilabe mukuzitukumula kwao ndipo iwo akukhalabe mchikondwerero pamene ali padzikoli lapansi ndiponso ngakhalenso atalowa Kumwamba limodzi ndi ife zitathazi, chikanakhala chosatikomera ife kuti Mulungu sakanachilora ichi kuchitika. Malonjezo a Mulungu, kuti Iye adzaweruza ndi kuononga onse amene adzazunza olungama, kuwazunza ndi mobaza awo, ndiponso kukhetsa magazi a oyera, ndichoyenerera ndiponso changwiro. 

Kukanakhala kulibe chiweruzo cha Mulungu cha ochimwa adzikoli lapansi, kodi sichikanakhala chosakomera olungama amene akhala miyoyo yawo yonse cifukwa cha Ambuye mukupilira kosaganizira zimene anali kukumana nazo mitundu yonse ya mazunzo ndiponso zobvuta? Choncho ndichoyenera chabe kuti Mulungu aweruze dzikoli lapansi. ngati dzikoli lapansi lakhala ngati dziko la pa nthawi ya Nowa, Mulungu adzapindamula dziko lonse ndi kuliononga. 

Cifukwa timakhulupilira mwa Ambuye, sitimasirira anthu adziko mwina mulimonse. Cifukwa Ambuye ananena kuti Iye adzaweruza dzikoli lapansi ndi kuponya Satana, Wosusa Khristu ndiponso omusatira Ake mmoto wa gehena, tonse tingapilire ndipo tingayembekeze. 

Dzikoli lapansi lasala mphindi imodzi yokha kuti lionongedwe, zonse kulingana ndi mauneneri a Mawu a Mulungu. Mdziko lonse lapansi, taona kale zidzindikiro zambiri zoonetsa kuyandikira kwa kubwera kwa miliri ya nthawi zomaliza. 

Mwina mosaoneka bwino monga chochitika cha El Nino ndiponso matenda atsopano monga Mad Cow Nthenda akudabwitsa dziko la matsiku ano. Matenda osapola amene anthu alibe mphamvu kuti awatheretse akudzaza dziko lapansi, monga muyezo waukulu, kumbuyoku chionongeko chosaganizirapo ngati njala yaikulu ndipo zivomezi zoopsa zoononga kukhuza dziko lonse lapansi. 

Ngati zinthu zonsezi zikuchitika, tiyenera kukhulupilira kuti Mulungu alipo, ndipo tikhale miyoyo yathu podziwa kuti Mulungu adzaweruza ndipo adzatsitsa onse amene akhala chabe ndi zokhumba za kuunjika chuma chao pamene ali mdzikoli lapansi. Uchimo wakhala uli kufalikira kwambiri mdziko la matsiku ano. Dzikoli ndilofunitsitsa kwambiri zinthu zapamwamba. Anthu naonso ali otangwanidwa ndi kukwatirana, kudya ndi kumwa, ndi kumanga manyumba awo kuti aike nzeru kudzakakhula—bwino kwa kuuzimu kwao. Dziko la matsiku ano ndi dziko limene mwamuna angachite uchimo wachigololo ndi mwamuna mzake, ndiponso si akazi achepa okha amene apheka ndi chilako-lako chao cha wina ndi mzache. (Aroma 1:27). 

Kodi dziko silinali tero mnthawi za Nowa? Mngakhale odziwa bwinobwino tanthauza la mawu akuti ‘sodomite.’ Pamene Sodomu ndi Gomara anaonongedwa, mkhalidwe wawo ukalibe chimodzimodzi ndi wa dziko la matsiku ano mu limene tsopano tikukhalamo. Dzikoli tsopano lakhala lonyansa ndiponso la uchimo, mopitilira milire kotero kuti Mulungu angagwetse moto ndi kuliotcha kukhala phulutsa lokha, ndipo lasandukiratu lodzazidwa ndi ziwanda. Aneneri Achinyengo Ayenera Kupohedwa


Aneneri achinyengo nthawi zonse amafunafuna kukhala n’katundu ndiponso kuziunjikira chuma kosasata malamulo, kubisala kumbuyo kwa wa chibale okhala payekha amene sali kubungwe la zipembezo zawo. “Ngati mukhulupilira mwa Yesu, mdzakhala a chuma, mdzakhala moyo wabwino, ndipo adzachilitsa matenda anu”—muyenera kudzindikira kumbuyo kwa boza lotero lililonse, cholinga chobisika chopezeramo katundu matsiku onse chikhalapo. 

Mu Koriya, namonso, chakhala kwa nthawi yaitali kuchokera pamene Chikristu chinataila chikhulupiliro chake choyamba ndipo chagwa, ndi mtundu uliwonse wa mphamvu za ziwanda kufalikira konsekonse mu dzina la Yesu. Ichi ndi choonadi cha Chikristu cha matsiku ano. Koma ku aneneri achinyengo amene amayeza chikhulupilira ndi kukahala ndi katundu wa dziko lapansi ndi kuchita ufiti ndiu Mawu a Mulungu, chiweruzo Chake choopsa cha gehena ndiponso cha miliri ya mbale 7 chiyemdekeza. 

Mulungu amatiuza kuti limodzi ndi amene amasocheretsa anthu ndiponso ndi amene asocheretsedwa ndi aneneri achinyengo onse adzaweruzidwa. Tisayangane kutsogolo kwa dzikoli ndi kulisatira. Tiyenera mmalo mwake kukhulupilira kuti cifukwa Mulungu ali moyo, onse amene, sakhulupilira mwa Yesu, asusana ndi Iye ndiponso azunza olungama onse adzaweruzidwa ndipo adzazugamulidwa ku imfa yosatha. Ndipo tiyeneranso kukhulupilira kuti atapita weruza chonchi dziko lapansi, Mulungu adzawapatsadi mphoto oyera cifukwa cha mazunzo ndi kupwetekedwa kwao kumene kunabwera cifukwa cha dzina la Yesu.