Sermons

[19-1] < Chivumbulutso 19:1-21 > Ufumu Umene Udzalamulilidwa ndi Wamphamvuyonse< Chivumbulutso 19:1-21 >

“Zimenezi zitatha, ndinamva mawu ofuula kumwamba ngati mawu a khamu lalikulu, akuti: “Tamandani Ya, anthu inu! Chipulumutso, ulemerero, ndi mphamvu ndi za Mulungu wathu, chifukwa ziweruzo zake ndi zoona ndi zolungama. Pakuti iye waweruza hule lalikulu limene linaipitsa dziko lapansi ndi dama lake, ndipo walibwezera chifukwa cha magazi a akapolo ake, amene hulelo linapha.” Nthawi yomweyo, ananenanso kachiwiri kuti: “Tamandani Ya, anthu inu! Utsiwochokera kwa iye udzafuka kwamuyaya.” Ndipo akulu 24 ndi zamoyo zinayi zija, anagwada pansi ndi kuwerama, n’kulambira Mulungu wokhalam pampando wachifumu, ndimawu akuti: “Ame! Tamandani Ya, anthu inu!” Komanso, kunamveka mawu ochokera kumpando wachifumu akuti: “Muzitamanda Mulungu wathu, inu nonse akapoloo ake, inu omuopa, olemekezeka ndi onyozeka omwe.” Kenako ndinamva mawu ngati a khamu lalikulu, omveka Ngati mkokomo wamadzi ambiri ndi mabingu amphamvu. Mawuwo anati: “Tamandani Ya, anthu inu, chifukwa Yehova Mulungu wathu, Wamphamvuyonse, wayamba kulamulira monga mfumu. Tiyeni tisangalale ndipo tikhale ndi chimwemwe chodzaza tsaya. Timupatse ulemerero, chifukwa ukwatiu wa Mwanawankhosa wafika, a ndipo mkazi wake wadzikongoletsa. Iye waloledwa kuvala zovala zapamwamba, zonyezimira ndi zoyera bwino, pakuti zovala zapamwambazo zikuimira ntchito zolungama za oyera.” Mngeloyo anandiuza kuti: “Lemba: Odala ndiwo amene aitanidwad ku phwando la chakudya chamadzulo la ukwatie wa Mwanawankhosa.” Anandiuzanso kuti: “Awa ndi mawu oona a Mulungu.” Pamenepo ndinagwada pansi n’kuwerama patsogolo pa mapazi ake kuti ndimulambire. Koma iye anandiuza kuti: “Samala! Usatero ayi! Inetu ndangokhala kapolo mnzako, ndi wa abale ako amene ali ndi ntchito yochitira umboni za Yesu. i LambiraMulungu, pakuti kuchitira umboni zaYesu ndiko cholinga cha maulosi.” Ndipo nditayang’ana ndinaona kumwamba kutatseguka, kenako ndinaona hatchi yoyera. Wokwerapo wake dzina lake linali Wokhulupirika ndi Woona. Iyeyo anali kuweruza ndi kumenya nkhondo mwachilungamo. Maso ake anali ngati lawi la motop ndipo pamutu pake panali zisoti zachifumu zambiri. Anali ndi dzina lolembedwa limene wina aliyense sanali kulidziwa, koma iye yekha. Iye anavala malaya akunja owazidwa magazi, ndipo dzina limene anali kutchedwa nalo linali lakuti Mawu a Mulungu. Komanso magulu ankhondo amene anali kumwamba, anali kumutsatira pamahatchi oyera, atavala zovala zapamwamba, zoyera bwino, za mbee! 15 M’kamwa mwake munali kutuluka lupanga lalitali lakuthwa, loti aphere mitundu ya anthu, ndipo adzawakusa ndi ndodo yachitsulo. Iye anali kupondapondanso m’chopondera mphesa cha mkwiyo waukulu wa Mulungu Wamphamvuyonse. Pamalaya ake akunja, ngakhale pantchafu yake, anali ndi dzina lolembedwa lakuti: 

MFUMU YA MAFUMU NDI MBUYE WA AMBUYE. 

Ndinaonanso mngelo ataimirira padzuwa. Iye anafuula ndi mawu okweza kwa mbalame zonse zouluka chapafupi m’mlengalenga, kuti: “Bwerani kuno, dzasonkhaneni ku phwando lalikulu la Mulungu la chakudya chamadzulo, kuti mudzadye minofu ya mafumu, ya akuluakulu a asilikali, ya amuna amphamvu, ya mahatchi ndi ya okwerapo ake, ndi minofu ya onse, yamfulu ndi ya akapolo, ya olemekezeka ndi ya onyozeka.”

Ndipo ndinaona chilombo, mafumu a dziko lapansi, ndi magulu awo ankhondo atasonkhana pamodzi kuti amenyane ndi wokwera pahatchi uja ndi gulu lake lankhondo. Koma chilombocho chinagwidwa limodzi ndi mneneri wonyenga uja, amene anachita zizindikiro pamaso pa chilombocho. Zizindikiro zimenezi anasocheretsa nazo olandira chizindikiro cha chilombo ndi olambira chifaniziro chake. Adakali amoyo, onse awiri anaponyedwa m’nyanja ya moto yoyaka ndi sulufule. Koma ena onse anaphedwa ndi lupanga lalitali la wokwera pahatchi, limene linatuluka m’kamwa mwake lija. Ndipo mbalame zonse zinakhuta minofu yawo.”Kusanthula


Ndime ya 1: “Zimenezi zitatha, ndinamva mawu ofuula kumwamba ngati mawu a khamu lalikulu, akuti: “Tamandani Ya, anthu inu! Chipulumutso, ulemerero, ndi mphamvu ndi za Mulungu wathu!”

Ndime inena za oyera kumatamanda Ambuye Mulungu ngati tsiku la ukwati wawo ndi Mwanawankhosa lafika pafupi. Ambuye Mulungu wathu oyera anawapatsa chipulumutso chao ndi ulemerero, kotero kuti iwo amuyamike Iye pa cifukwa choyenera. Oyera okwatulidwa mmtambo choncho apitilizabe kumayamika Ambuye Mulungu, cifukwa chachikulu kwambiri ndi chisomo Chake chowaombola kuchoka ku machimo awo ndi kuchionongeko chao chosalephera. 

Mawu akuti “alleluia” kapena “hallelujah” ndi mawu osakanikana olumikiza mawu a mu Chiheberi a “halal,” kutanthauza kuyamika, ndipo “Yah” kutanthauza “Yehova”—tanthauzo lake, choncho, ndi “yamikani Yehova” Makamaka, mu Masalimo 113-118 mu Pangano la Kale otchedwa kuti “Hallel wa ku Eguputo,” ndipo mu Masalimo 146-150 otchedwa “Masalimo a Hallel.” 

“Masalimowa a Hallel” ndi manyimbo amene aphatikiza cimwemwe ndi chisoni cha anthu a Chiyuda, owapatsa mphamvu mnthawi za chisoni ndiponso mu masautso, ndi kuimba ngati nyimbo za cimwemwe mnthawi za chipulumutso ndiponso mkupambana. Nyimbozi zinali kuimbidwanso mnthawi iliyonse yoyamikira “hallelujah” ingaimbidwe kwa Mulungu Yekha. Cifukwa ndi chakuti chiweruzo cha Ambuye cha miliri yaikulu choperekedwa pa dzikoli lapansi n’choona ndiponso cholungama, ndipo cifukwa chipulumutso, mphamvu, ndi ulemerero ndi za Mulungu Yekha. 


Ndime ya 2: “chifukwa ziweruzo zake ndi zoona ndi zolungama. Pakuti iye waweruza hule lalikulu limene linaipitsa dziko lapansi ndi dama lake, ndipo walibwezera chifukwa cha magazi a akapolo ake, amene hulelo linapha.”

Kunena kuti Ambuye Mulungu adzabwezera oyera pothira miliri yambale 7 pa onse azipembezo a dziko lapansi ndiponso pa osakhulupilira onse ndi chiweruzo cha zoona ndiponso cholungama cha Mulungu. Cifukwa azipembezo a padzikoli lapansi apha atumiki a Mulungu opanda uchimo ndiponso olungama, iwo, mobwezera, ayenerera kugamulidwa ku imfa ya muyaya ndi Mulungu. 

Kodi atumiki a Mulungu achita chinthu china padzikolin lapansi choyenerera kuti aphedwe ndi azipembezo za padzikoli lapansi? Ndithudi ai! Komabe azipembezo onse a dziko lapansi agwirizana mu maganizo awo kuti aphe ana a Ambuye Mulungu. Choncho, kuthira kwa miliri yambale 7 pa okuphawa kwa Mulungu n’koyenerera, kumenenso kumaonetsa chilungamo cha Mulungu. 


Ndime ya 3: Nthawi yomweyo, ananenanso kachiwiri kuti: “Tamandani Ya, anthu inu! Utsi wochokera kwa iye udzafuka kwamuyaya!”

Oyera amatamanda Mulungu mmtambo cifukwa tsiku la ukwati wawo ndi Yesu, amene akhala Mwanawankhosa, la yandikira. 

“Utsi wochokera kwa iye udzafuka kwamuyaya.” Uwu uimilira utsi otuluka kuchoka mdzikoli lapansi kuononga ndiponso kuotcha ndi miliri yaikulu ya mbale 7 yothiridwa ndi Mulungu. Umationetsa kuti dzikoli lapansi silidzabwererapo kuchoka ku kuonongedwa kwake cifukwa chionongeko chake chidzakhala chosapola ndiponso chamuyaya. 


Ndime ya 4: Ndipo akulu 24 ndi zamoyo zinayi zija, l anagwada pansi ndi kuwerama, n’kulambira Mulungu wokhalam pampando wachifumu, ndimawu akuti: “Ame! Tamandani Ya, anthu inu!” 

Choona chakuti tsiku la ukwati wa oyera ndi AmbuyeYesu layandikira ndi chinthu cha ulemerero cimene akulu 24 ndiponso zamoya zinayi Kumwamba zikulambira ndi kumayamika Ambuye Mulungu pampando Wake wachifumu. Ichi ndicho cifukwa atumiki onse a Mulungu amayamika Mulungu mmtambo. 


Ndime ya 5: Komanso, kunamveka mawu ochokera kumpando wachifumu akuti: “Muzitamanda Mulungu wathu, inu nonse akapoloo ake, inu omuopa, olemekezeka ndi onyozeka omwe!”

Cifukwa tsiku la ukwati wa Mwanawankhosa ndi oyera n’cimwemwe chachikulu chosaneneka cha atumiki Ake onse ndi oyera amene anapulumutsidwa pokhulupilira mwa Ambuye Mulungu, mawu ochokera kumpando wa wachifumu owauza kuti amutamande Mulungu. Tsopano nthawi yabwera ya atumiki a Mulungu ndi oyera Ake onse kuti akondwere ndi kutamanda Ambuye. 


Ndime ya 6: Kenako ndinamva mawu ngati a khamu lalikulu, omveka Ngati mkokomo wamadzi ambiri ndi mabingu amphamvu. Mawuwo anati: “Tamandani Ya, anthu inu, chifukwa Yehova Mulungu wathu, Wamphamvuyonse, wayamba kulamulira monga mfumu!”

Ndimeyi imatiuza kuti monga mmene nthawi ya kulamulira kwa Ambuye Mulungu ya yandikira, tsopano ndi nthawi ya oyera ndi atumiki Ake kuti alandire mtendere wosatha, cimwemwe, ndiponso madalitso amene akusefukira ngati mtsinje. Ichi ndicho cifukwa iwo amatamanda Ambuye Mulungu. Oyera amatamanda Mulungu wathu mmtambo ngakhale kuti miliri yaikulu ipitilizabe padzikoli lapansi cifukwa nthawi yabwera yoti iwo alamulira mwa Ambuye Mulungu—imene ndi, tsopano nthawi yoti Mulungu alemekeze oyera Ake onse. Mkokomo wa oyera kutamanda panthawi uli ngati mkokomo wa kugunda mumabingu ndiponso wa madzi ambiri. Mgonero wa ukwati wa Ufumu wa Ambuye umayamba chonchi ndi kutamando kokongola kwa oyera. 


Ndime ya 7: “Tiyeni tisangalale ndipo tikhale ndi chimwemwe chodzaza tsaya. Timupatse ulemerero, chifukwa ukwatiu wa Mwanawankhosa wafika, ndipo mkazi wake wadzikongoletsa.”

Tsopano kuti miliri ya mbale 7 yobweretsedwa ndi Mulungu ilikutha, ndimeyi imatiuza kuti nthawi ya oyera onse yabwera kuti akondwere ndiponso asangalale. Apa oyera ndi okondwera ndiponso osangalala cifukwa tsiku labwera kuti iwo akwatiwe ndi Ambuye ndi kukhala mu Ufumu Wake. Kuti akhale ndi oyera, Ambuye Muloungu wathu anakonza Kumwamba Kwake kwa Tsopano ndi Dziko lapansi, mzinda woyera ndi minda yake, ndiponso ulemerero wonse ndi chuma, ndipo Iye amawayembekeza. Kuchokera pa nthawiyi mpaka kutsogoloku, oyera adzakhala nfi Ambuye kwa muyaya. 


Ndime ya 8: Iye waloledwa kuvala zovala zapamwamba, zonyezimira ndi zoyera bwino, pakuti zovala zapamwambazo zikuimira ntchito zolungama za oyera.

Ambuye anapatsa oyera zobvala zatsopano, zimene zimapangidwa ndi salu yonyezimira. Wina aliyense amene akhala n’kutumikira Ambuye Mulungu amabvekedwa mzobvalazi. Mulungu amabvalika oyera, mmawu ena, mzobvala za Kumwamba. Zobvalazi za Kumwamba si zonana ndi thukuta. Ichi chimatiuza choona chakuti takhala akwatibwi a Mwanawankhosa osati cifukwa cha mphamvu yopangidwa-ndi munthu ndiponso zoziunjikira, koma cifukwa cha chikhulupiliro chatu mu uthenga wa madzi ndi Mzimu wopatsidwa ndi Ambuye Mulungu. 

Mosiyanitsa ndi zobvala zofiira kwambiri ndiponso zoyera zobvalidwa ndi Wosusa Khristu, salu zonyizimirazi ndi zonyezimira za pamwamba zinali kugwiritsidwa nchito pothunga zobvala za ansembe ndi mafumu. Zosagwira thukuta, zoyera bwino, zobvala zonyezimira zimationetsa kuti amene abvekedwa mchisomo cha Mulungu ndiponso muchilungamo Chake tsopano akhala anthu Ake. 

Ndi mawu akuti, “pakuti zovala zapamwambazo zikuimira ntchito zolungama za oyera,” atanthauza kuti amene akhala oyera mwa chisomo cha chipulumutso chopatsidwa ndi Ambuye Mulungu anapereka ulemerero kwa Mulungu ndi kuphedwa kwao ndi Wosusa Khristu ndi omusatira ake mkuteteza chikhulupiliro chao. “ntchito zolungama,” mmawu ena, saimilira chilungamo mwa Chilamulo, koma mkuphedwa kwa oyera mkuteteza chikhulupiliro chao. Chimodzmodzi, akwatibwi onse a Yesu Khristu a mnthawi zomaliza ndi ophedwe amene, kuti ateteze chikhulupiliro chao mwa Ambuye, aima ndi kumenyana ndi Wosusa Khristu ndi omusatira pamene anali padzikoli lapansi. 

Kuti akonzekera za chikhulupiliro chao cha kuphedwa, oyera onse ayenera kulimbitsidwa kwa zaka zoyemba zitatu ndi hafu za Chisautso Cahchikulu, cifukwa ngati zakazi zitatu ndi hafu zapita, adzaphedwadi. 


Ndime ya 9: Mngeloyo anandiuza kuti: “Lemba: Odala ndiwo amene aitanidwad ku phwando la chakudya chamadzulo la ukwatie wa Mwanawankhosa.” Anandiuzanso kuti: “Awa ndi mawu oona a Mulungu.”

Ngati miliri ya Mulungu yatha mdzikoli lapansi, Ambuye Mulungu adzaitana oyera onse ku mgonero ukwati wa Mwanawankhonsa (ku Ufumu womangidwa ndiponso wolamililidwa ndi Ambuye), ndipo Iye adzawalora kuti akhale mu Ufumu wa Khristu. Onse amene adzaitanidwa ku mgonero wa ukwati wa Mwanawankhosa apa ndi odala. Mulungu wathu anatiuza kuti Iye sadzalephera kukwanilitsa Mawuwa alonjezo. Tsiku lidzabweradi pamene oyera adzakwatilidwa ndi Ambuye. Ambuye athu adzabweranso padzikoli lapansi kudzatenga akwatibwi Ake, amene anayeretsedwa ku machimo awo onse pokhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu. Ndipo Ambuye Iye adzakhala ndi amkwatibwi Ake kwa muyaya mu Ufumu Wake. 

Mugwirizana wa oyera ndi Ambuye udzakwanilitsidwa ngati oyera akwatulidwa ndi Khristu, pa nthawi imene iwo adzalandira ulemerero osatha ndiponso mphoto mu Ufumu wa zaka chikwi chimodzi. Haleluya! Ndiyamika ndi kuthokoza Ambuye Mulungu amene anatilenga ife anthu Ake. 


Ndime ya 10: Pamenepo ndinagwada pansi n’kuwerama patsogolo pa mapazi ake kuti ndimulambire. Koma iye anandiuza kuti: “Samala! Usatero ayi! Inetu ndangokhala kapolo mnzako, ndi wa abale ako amene ali ndi ntchito yochitira umboni za Yesu. i LambiraMulungu, pakuti kuchitira umboni za Yesu ndicho cholinga cha maulosi.”

Oyera ayenerera kupereka maulemerero onsewa kwa Ambuye Mulungu Yekha. Umodzi amene ayenerera kulandira matamando ndiponso kuyamika ndi Mulungu Mtatu Yekha. 

Mawu akuti, “pakuti kuchitira umboni za Yesu ndicho cholinga cha maulosi,” atanthauza kuti maumboni ndi maulosi a za Yeus abwera kupyolera mu Mzimu Woyera. 


Ndime ya 11: Ndipo nditayang’ana ndinaona kumwamba kutatseguka, kenako ndinaona hatchi yoyera. Wokwerapo wake dzina lake linali Wokhulupirika ndi Woona. Iyeyo anali kuweruza ndi kumenya nkhondo mwachilungamo.

Ngati nthawi zomaliza zabwera Ambuye Mulungu athu, wokwera pa hatchi yoyera, adzamenyana ndi Satana mwachilungamo Chake ndipo adzamumanga iye pomuponya iye mu dzenje lolowera kuphompho ndipo mng’anjo ya moto.

Apa, dzina la Yesu Khristu ndi “Wokhulupirika” ndi “Woona”. Mawu akuti “Wokhulupirika” kutanthauza kuti Khristu ndi wokhulupirika, akuonetsa kukhulupirika Kwake ndiponso ulemu, pamene mawu akuti “Woona,” kutanthauza kuti Iye ndi omasuka kuchoka ku chinyengo, amatiuza kuti Khristu adzapamabana Wosusa Khristu mwachiweruzo chachilungamo cha Mulungu. 


Ndime ya 12: Maso ake anali ngati lawi la moto ndipo pamutu pake panali zisoti zachifumu zambiri. Anali ndi dzina lolembedwa limene wina aliyense sanali kulidziwa, koma iye yekha.

Kunena kuti maso a Ambuye ali “ngati lawi la moto” amatiuza kuti Iye ali ndi mphamvu yoweruza aliyense. Mawu akuti, “pamutu pake panali zisoti zachifumu zambiri,” mnjira ina, atanthauza kuti Ambuye athu nthawi zonse amapamabana Satana mkumenyana Kwake ndi iye, cifukwa iye ndi Mulungu woyamba ndiponso wa mphamvuyonse. 


Ndime ya 13: Iye anavala malaya akunja owazidwa magazi, ndipo dzina limene anali kutchedwa nalo linali lakuti Mawu a Mulungu.

Ambuye Mulungu wathu adzabwezera oyera adani awo pakuwaweruza adani Akewa, amene akhala ali kususana ndi Iye, ndi mkwiyo Wake waukulu. Mulunguyu ndi Yesu Khristu Iyeyekha. Monga mmene Iye analonjezera ndi Mawu Ake, Ambuye athu anabweradi padzikoli lapansi mthupi la munthu, anabatizidwa ndi Yohane kuti anyamule machimo onse adziko lapansi, anayanyamula pa Mtanda, ndipo anapanga kuti machimo a anthu onse azimiririke. 

“Malaya akunja owazidwa magazi.” Magaziwa saimilira magazi ake a Khristu. Aimilira magazi a adani Ake kuwazidwa ku malaya akunja a Ambuye pamene Iye ali kubweretsa chiweruzo Chake cha mkwiyo oopsa pa iwo ndi kuwapondaponda ndi mwendo Wake wa mphamvu. 

“Mawu a Mulungu” aimilira mkhalidwe wa Yesu. Cifukwa Ambuye athu akuchita china chilichonse mwa Mawu Ake a mphamvu, Iye atchedwa kuti “Mawu a Mulumngu.” 


Ndime ya 14-16: Komanso magulu ankhondo amene anali kumwamba, anali kumutsatira pamahatchi oyera, atavala zovala zapamwamba, zoyera bwino, za mbee! M’kamwa mwake munali kutuluka lupanga lalitali lakuthwa, loti aphere mitundu ya anthu, ndipo adzawakusa ndi ndodo yachitsulo. Iye anali kupondapondanso m’chopondera mphesa cha mkwiyo waukulu wa Mulungu Wamphamvuyonse. Pamalaya ake akunja, ngakhale pantchafu yake, anali ndi dzina lolembedwa lakuti: MFUMU YA MAFUMU NDI MBUYE WA AMBUYE. 

Msilikari wa Ambuye tsiku ndi tsiku amatumikira ntchito za Iye, obvekedwa mu chisomo Chake cholemekezeka. 

Mulungu adzaweruza dzikoli ndi Mawu Ake otuluka mkamwa Mwake. Ambuye athu tsiku ndi tsiku akhala otilonjeza ndi Mawu a mkamwa Mwake, ndipo Iye tsiku ndi tsiku amakwanilitsa malonjezowa mwa mphamvu Yake. Amene amaweruza dziko ndi kuononga Satana ndi Yesu Khristu, Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye. 


Ndime ya 17: Ndinaonanso mngelo ataimirira padzuwa. Iye anafuula ndi mawu okweza kwa mbalame zonse zouluka chapafupi m’mlengalenga, kuti: “Bwerani kuno, dzasonkhaneni ku phwando lalikulu la Mulungu la chakudya chamadzulo,”

Dzikoli lapansi, limodzi ndi Satana ndiponso omsatira ake, pothera lidzaonongedwa ndi Yesu Khristu. Baibulo limanena za chionongeko cha dzikoli ngati phwando lalikulu la Muolungu. 


Ndime ya 18: “kuti mudzadye minofu ya mafumu, ya akuluakulu a asilikali, ya amuna amphamvu, ya mahatchi ndi ya okwerapo ake, ndi minofu ya onse, yamfulu ndi ya akapolo, ya olemekezeka ndi ya onyozeka.”

Mawuwa amatiuza kuti cifukwa dziko lonse ndipo wina aliyense mmenemo adzaphedwa pa nthawi imene miliri yaikulu ya Ambuye Mulungu idzathera, mabalame zouluka m’mlengalenga zidzazaza mimba zawo pakudya mathupi awo akufa. Zidzachita tero cifukwa Mulungu adzathira miliri yaikulu ya mbale 7 padzikoli lapansi. Ambuye athu anatiuza kuti, “Kulikonseko kumene kuli thupi lakufa, ziwombankhanga zimasonkhana komweko (Mateyu 24:28).” Mnthawi yakutha kwa dziko lapansi, kudzakhala chionongeko chokhachokha, imfa, ndiponso chilango cha mgehena ku ochimwa. Koma ku oyera, kudzakhala dalitso lokhala mu Ufumu wa Khristu. 


Ndime ya 19: Ndipo ndinaona chilombo, mafumu a dziko lapansi, ndi magulu awo ankhondo atasonkhana pamodzi kuti amenyane ndi wokwera pahatchi uja ndi gulu lake lankhondo. 

Mpaka kumapeto awo enieni, Wosusa Khristu, atumiki a Satana, ndi omusatira ake adzasusana ndi atumiki a Mulungu ndi oyera Ake ndipo adzafuna kuti awapambane. Koma cifukwa Ambuye ndi Mfumu ya mafumu, Iye adzamumanga Wosusa Khristu ndi aneneri onyenga, adzawaponya mng’anjo ya moto, ndikupha atumiki ake onse ndi lupanga la Mawu Ake. 


Ndime ya 20: Koma chilombocho chinagwidwa limodzi ndi mneneri wonyenga uja, amene anachita zizindikiroo pamaso pa chilombocho. Zizindikiro zimenezi anasocheretsa nazo olandira chizindikiro cha chilombo ndi olambira chifaniziro chake. Adakali amoyo, onse awiri anaponyedwa m’nyanja ya moto yoyaka ndi sulufule.

“Chilombo” apa chiimilira Wosusa Khristu. “Mneneri onyenga” ndi mtumiki wa Wosusa Khristu amene, pochita zodabwitsa ndiponso zionetsero, adzatembenura anthu kochoka ku chikhulupiliro mu Mawu achoonadi. Ambuye Mulungu wathu adzaononga Satana, Chilombo (Wosusa Khristu), mneneri onyenga, ndi osatira Satana amene anakhala ali kulambira fano la Wosusa Khristu ndipo akhala ali kususana ndi Mulungu, kususana ndi oyera, kususana ndi uthenga wa madzi ndi Mzimu. 

“M’nyanja ya moto yoyaka ndi sulufule” iimilira gehena. Gehena ndiyotsiyana ndi dzenje lolowera kuphompho. Pamene dzenje lolowera kuphompho ndi kumene mphamvu zamdima za Satana zimasungidwa kwa ka nthawi zomangidwa, nyanja ya moto ndi malo a chilango chao chosatha. Makamaka, moto ndi sulufule, zakhala zili kugwiritsidwa ntchito mu Baibulo tsiku ndi tsiku ngati zida za chilango ndiponso chiweruzo cha Mulungu.

Kutapita kuonongedwa kwa dzikoli lapansi, Ambuye athu adzabweranso padzikoli lapansi ndi oyera, kudzaononga Satana ndi atumiki ake poyamba, ndiyeno kudzatsegura Ufumu wa Khristu. Oyera ndiyeno adzakhala ndi kulamulira ndi Ambuye mu Ufumu wa Khristu kwa zaka chikwi chimodzi zikubweraku. 


Ndime ya 21: Koma ena onse anaphedwa ndi lupanga lalitali la wokwera pahatchi, limene linatuluka m’kamwa mwake lija. Ndipo mbalame zonse zinakhuta minofu yawo.

Dzikoli linalengedwa ndi Mawu otuluka mkamwa mwa Ambuye Mulungu wathu; chimodzimodzi, adani a Mulungu adzaonongedwa ndi Mawu a chiweruzo otuluka mkamwa Mwake. Ndiyeno Ufumu wa Yesu Khristu udzakhazikitsidwa padzikoli lapansi. Choncho, oyera, ayenera kuika chiyembekezo chao mu Ufumu wa Khristu ndi kupereka ulemerero kwa Mulungu pomenyana ndi Satana, Wosusa Khristu ndi omusatira ake, ndiponso polora kuphedwa kwao mwa chikulupiliro.