Sermons

[19-2] < Chivumbulutso 19:1-21 > Ndi Olungama Okha Amene Angadikhire mu Chiyembekezo KutiKhristu Abwerenso< Chivumbulutso 19:1-21 >


Mchapitala yomwe tapita, tinaona mmene Mulungu adzabweretsera miliri Yake yoopsa padzikoli lapansi. Mu chipatalayi, tsopano tikuona kuti Khristu ndi gulu Lake la ankhondo olemekezeka akumenyana ndi kupambana gulu la nkhondo la Wosusa Khristu, kuponya chilombo ndi atumiki ake mnyanja ya moto, kupha ena onse ankhondo a Wosusa Khristu ndi lupanga la Mawu otuluka mkamwa mwa Ambuye, ndipo chonchi ndimmene adzathetsera nkhondo Yake yomanyena ndi Satana. 

Mutu wa chapitalayi ungagawidwe mu mitu itatu ikulu ikulu: 1) kutamanda Mulungu kwa oyera okwatulidwa cifukwa cha kubweretsa chiweruzo cha miliri yaikulu padzikoli lapansi; 2) kulengeza kwa kubwera kwa mgonero wa ukwati wa Mwanawankhosa; ndipo 3) kutsika kwa Ambuye kuchokera Kumwamba limodzi ndi gulu la nkhondo la Yesu Khristu. 

Tonse tiyenera kudzindikira kuti Mulungu adzakwanilitsadi kosadzengereza ndipo posachedwa zinthu zonse zimene Iye analankhula kwa ife kupyolera mu Buku la Chivumbulutso. Chiweruzo cha Mulungu!


Onse amene okhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu ndipo ndimene anakhala anthu a Mulungu kupyolera muchikhulupiliro adzakhala ali kumutamanda Iye cifukwa cha kuwapulumutsa kuchoka ku machimo awo onse a mdziko lapansi. Tiyeni tiyangane mndime ya 3-5: “Nthawi yomweyo, ananenanso kachiwiri kuti: ‘Tamandani Ya, anthu inu! Utsi wochokera kwa iye udzafuka kwamuyaya.’ Ndipo akulu 24 ndi zamoyo zinayi zija, anagwada pansi ndi kuwerama, n’kulambira Mulungu wokhala pampando wachifumu, ndimawu akuti: “Ame! Tamandani Ya, anthu inu!” Komanso, kunamveka mawu ochokera kumpando wachifumu akuti: ‘Muzitamanda Mulungu wathu, inu nonse akapoloo ake, inu omuopa, olemekezeka ndi onyozeka omwe!’” 

Aheberi 9:27 imatiuza kuti, “Monga mmene zilili ndi anthu kuti amayembekezera kufa kamodzi kokha, kenako n’kudzalandira chiweruzo.” Munthu ayenera kuweruzidwa pamaso pa Mulungu kamodzi kokha, kugumula kwa chiweruzochi ndi kothera ndipo si kudzabwezedwa. Ndi chiweruzo Chake cha kamodzi-kokha cha wina aliyense cifukwa cha machismo ake, mmawu ena, Mulungu adzapereka chiweruzo Chake chosatha poponya ochimwa mmoto umene ukuyaka kwa muyaya. Ichi ndicho cifukwa baibulo imatiuza kuti, “utsi wochokera kwa iye udzafuka kwamuyaya.” 

Anthu ena angaganize ndi kunena kuti, “ngati inu mwafa, uku ndi kutha komweko.” Koma awa ndimaganizo ake a munthu, osati maganizo a Mulungu. cifukwa wina aliyense ali n’zonse thupi ndi moyo, mwina athu akhulupilira mwa Mulungu kapena ai, onse adziwa kwenikweni kuti Mulungu alipo, ndi kuti posachedwa kapena pafupifupipa onse adzaweruzidwa cifukwa cha machimo awo pamaso pa Iye. 

Monga mmene ufumu wa mizimu ya anthu, iwo akudziwa kuti Mulungu, ngakhale kuti saoneka ndi maso awo, alipobe. Ufumu umene ungaoneke ndi maso a anthu a thupi sukhala kwa muyaya, koma ulipo ufumu wosatha wa choonadi, osaoneka ndi maso athu. Kulemera kwa katundu padzikoli lapansi ndinso kungoganizira za chuma chokha ndiponso kufuna funa katundu si chingakhale cifukwa cha munthu chokha chokhala; cholinga choona ndi cholowa mu ufumu wosatha wa dalitso pakudziwa Mulungu, Mlengi wa dziko lonse, ndiponso podziwa ndi kukhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu wopatsidwa ndi Iye. 

Osati ife tiyenera kudziwa kokha zimene anatiuza Mulungu, koma tiyeneranso kukhulupilira mu zimenezo. Si tiyenera kukhatsirizira mgehena pokhulupilira ndiponso olimbika mumaganiza athu athu okha. Tisanakumane ndi kuzunzidwa kosatha kwa machimo athu, tiyenera kukhululukidwa ku machimo anthu onse ndi kulandira moyo osatha pokhulupilira, pamene tikukhala mdzikoli lapansi tsopano, mu uthenga wa madzi ndi Mzimu wopatsidwa ndi Yesu.

Ku wina aliyense, moyo padzikoli lapansi ndi waufupi kwambiri. Monga mmene dzuwa limatulukira ndiponso limalowera tsiku ndi tsiku, ulendo waufupi wa miyoyo yathu umatha mwamsanga, wosabala zipatso ndiponso opanda phindu, ngati ndipamene takhala tili kuthamanga ngati mbalame. Ngati kuti mkanakhala zaka 100, simkananenadi kuti mwakhala kwa nthawi yaitali. 

Ngati mwachotsako nthawi zing’ono zing’ono za moyo wathu wa tsiku ndi tsiku, nthawi zotero zinagwiritsidwa nchito pakugona, pakudya, kupita n’kusamba, ndiponso kuchita zinthu zina zache zotero, kuchokera pa nthawi yonse ya moyo wanu, inu mwakhaladi ndi nthawi yaing’ono. Pamene muli kuona zinthu zimene munaziona kale kuchokera pamene mtabadwa, ndipamene mmakumana ndi anthu amene munaonanapo kale, nsinsi zanu zonse ndi imvi, ndiponso mwadzizizi muzazipeza kuti mwakumana ndi mapeto anu. 

Cifukwa cimene moyo wathu ife oyera si opanda phindu ndi cifukwa ife, tabadwira mdzikoli lapansi, takumana ndi Ambuye amene wabwera kwa ife kupyolera mu uthenga wa madzi ndi Mzimu, takhulupilira mwa Iye, ndipo choncho talandira chikhululukiro cha machimo athu onse. Ndife a mwai ndiponso othokoza! Kukanakhala kupanda Ambuye amene anabwera kwa ife kupitala mu madzi ndi Mzimu, tonse tikanagamuludwa kulowa mu moto wosatha ndi kubvutika mmenmo. 

Paliponnse pamene ndaganiza za ichi, chimandidetsa nkhawa, ndipo Ndimabwera kudzathokozanso Ambuye. Gehena, imene anakhalako cifukwa cha Satana, ndimalo opondeleza kwambiri, kumene mazunzo ndi aakulu kwambiri kumene wina angakonde kufa, koma sangathe kuchita tero. Ndimalo kumene moto ndi sulufule ziyaka kwa muyaya. 

Kuti tiziwe uthenga wa madzi ndi Mzimu wopatsidwa ndi Yesu moyenera, ndiponso n’kulandira Mzimu Woyera, wina poyamba ayenera kukumana ndi mtumiki wa Mulungu amene anakumana kale ndi uthengau wa madzi ndi Mzimu ndiponso ndi wina amene anakumana ndi uthengau wa madzi ndi Mzimu ndipo amene anabadwa kale mwatsopano. Kukhala ngati Mkristu, aliyense amene afuna kupeza yankho funso la kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu ndiponso lolandira Mzimu Woyera angathe onse pokhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu. 

Baibulo imatiuza kuti Mzimu wa Mulungu wupatsidwa ngati mphatso ku onse amene analandira chikhululukiro cha uchimo pokhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu (Machitidwe 2:38). Ndi okhawo amene ali ndi Mzimu Woyera mmitima yawo pokhululukidwa kwa machimo awo onse kupitala muchikhulupiliro chao mu uthenga wa madzi ndi Mzimu angatchedwa kuti ali ndi chikhulupiliro choyenera mwa Yesu, ndiponso ndi okhawo ali ndi chikhulupilirochi angalowe mu Ufumu wa Mulungu (Yohane 3:5). Mwina wina ndi odalitsika kapena otembeleredwa chimakhala pa mwina wina analandira chikhululukiro cha uchimo pokhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu kapena ai.Atavala Zovala Zapamwamba, Zoyera Bwino Mbee


Onse amene aganiza za tsogolo lawo ndipo akufuna kuthesa bvuto la kukhululukidwa kwa machimo awo ndi amene ali ndi nzeru ndiponso ndi odala. Ngakhale wina akhale moyo odzaza ndi zolakwika zambiri, ngati iye akhulupilira mu uthenmga wa madzi ndi Mzimu ndipo alandira chikhululukiro cha uchimo ndi mzimu Woyera mmtima, ndiyeno munthuyu akhala moyo okwanilitsa bwino pa zonse. 

Chivumbulutso 19:4-5 ikuti, “Ndipo akulu 24 ndi zamoyo zinayi zija, anagwada pansi ndi kuwerama, n’kulambira Mulungu wokhala pampando wachifumu, ndimawu akuti: “Ame! Tamandani Ya, anthu inu!” Komanso, kunamveka mawu ochokera kumpando wachifumu akuti: ‘Muzitamanda Mulungu wathu, inu nonse akapoloo ake, inu omuopa, olemekezeka ndi onyozeka omwe!’”

Apa, mawu akuti “(ku) opa Iye” atanthauza kumvomereza Mawu a Yesu Khristu mmtima wa wina ndi kukhala kulingana ndi utsogoleri Wake. Ndi okhawo amene anakhululukidwa machimo awo anamuone ndiponso kumutamanda Mulungu mu Ufumu wa Kumwamba. Koma ku onse amene sanalandire chikhululukiro cha machimo awo adzazunzidwa mu moto oyaka wa mgehena ndipo otembereredwa. 

Tiyeni tipitilize ndi ndime ya 6-9: “Kenako ndinamva mawu ngati a khamu lalikulu, omveka Ngati mkokomo wamadzi ambiri ndi mabingu amphamvu. Mawuwo anati: “Tamandani Ya, anthu inu, chifukwa Yehova Mulungu wathu, Wamphamvuyonse, wayamba kulamulira monga mfumu!” “Tiyeni tisangalale ndipo tikhale ndi chimwemwe chodzaza tsaya. Timupatse ulemerero, chifukwa ukwati wa Mwanawankhosa wafika, ndipo mkazi wake wadzikongoletsa.” Iye waloledwa kuvala zovala zapamwamba, zonyezimira ndi zoyera bwino, pakuti zovala zapamwambazo zikuimira ntchito zolungama za oyera.” Mngeloyo anandiuza kuti: “Lemba: Odala ndiwo amene aitanidwa ku phwando la chakudya chamadzulo la ukwati wa Mwanawankhosa.” Anandiuzanso kuti: ‘Awa ndi mawu oona a Mulungu.’”

Apa ikunena kuti Mtumwi Yohane anamva mawu otamanda, mawu ngati a khamu lalikulu, phokoso la madzi ambiri, ndiponso mawu a kugunda kwa mabingu kwakukulu. Mawu anali mawu a onse amene analandira chikhululukiro cha uchimo anasonkhana pamodzi ndi kumatamanda Mulungu. Nyimboyi ya matamando inapangidwa ndi, poyamba pa zonse, kutamanda Mulungu powalora iwo khala pansi paulamulilo wa Mulungu Wamphamvuyonse, kuti alamulilidwe ndi Iye. Zonse zinthuzi zapanga oyera kukhala okondwera kwambiri ndiponso osangalala koposa ndi kupereka ulemerero kwa Mulungu. Choncho, sangalephera koma kumatamanda Iye, kufuula, “Tiyeni tisangalale ndipo tikhale ndi chimwemwe chodzaza tsaya ndipo timupatse Iye ulemerero.” 

Kachiwiri, oyera anapitiliza ndi matamando awo: “chifukwa ukwati wa Mwanawankhosa wafika, ndipo mkazi wake wadzikongoletsa. Iye waloledwa kuvala zovala zapamwamba, zonyezimira ndi zoyera bwino, pakuti zovala zapamwambazo zikuimira ntchito zolungama za oyera.” Kodi ichi chitanthauza nciani? Chitanthauza kuti monga mmene Iye analonjezera anthu, Yesu adzabweranso padzikoli lapansi, kukwatira onse amene analandira Mzimu Woyera pokhulupilira mwa Iye ndiponso pobadwa mwatsopano, ndipo adzakhala ndi iwo kwa muyaya. 

Chikwati ndi kukhala pamodzi kwa mkwati ndi mkwatibwi. Ngati Yesu abweranso pa dzikoli lapansi, mmawu ena, Iye angabwere amvomera ndi kukhala pamodzi ndi okhawo anabadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Ndipo chitanthauza kuti Iye adzakhazikitsa Ufumu Wake wa zaka Chikwi chimodzi ndi Kumwamba kwa Tsopano ndiponso Dziko lapansi kuti akhale ndi oyuera kwa muyaya. Ulemerero wa akwatibwi okhala ndi Mkwati ndi chinthu chachikulu kwambiri cymene sitingathe kufotokazo. Koma poganizira pa cimenechi, mitima yathu imatupa ndi chikobdwerero. 

Ngati dziko lapansi mmene Yesu Khristu adzalamulira labwera, akwatibwi Ake adzakhala okondwera kwambiri, kupilira pamene mawu angathe kufotokoza. Adzakha okondera kotani ngati iwo alamulilidwa ndi M’busa wa Bwino? Pakuti Yesu Khristu ndi mkwati wa bwino kwambiri ndiponso wanghwiro. Iye adzalamulira mu Ufumu wa Kumwamba. Uthenga Umodzi ndiponso Okhawo Umene Ungakuperekeni Kumwamba


Kuti wina alandire Mzimu Woyera ndi kulowa Kumwamba, iye ayenera kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi magazi Ake. Cifukwa Ambuye athu anabwera padzikoli lapansi kuti apulumutse ochimwa onse kuchoka ku machimo awo onse potenga machismo onse otero a anthu pa Iyeyekha, Iye anabatizidwa ndi Yohane. Atalandire chonchi ubatizo Wake, Yesu Iyeyekha ndiyeno anapachikidwa pa Mtanda mmalo athu, anaweruzidwa cifukwa cha machimo athu onse, anaukanso ku akufa, ndipo anakhala Ambuye wa chipulumutso chosatha wa onse amene akhulupilira.

Ambuyeyu tsopano adzabweranso padziko, kulandira anthu Ake amene anakhala amkwatibwi Ake kupitira mchikhulupiliro, ndi kukhala ndi iwo kwa muyaya. Onse amene akhala amkwatibwi Ake tsopano adzakhala limodzi ndi Ambuye pa dziko lapansi la tsopano, dalitso lolemekezeka ndiponso lolemekeza amkwatibwi. Ana opulumutsidwa a Mulungu ndimmene adzaperekera ulemerero kwa Yesu Khristu pomutamanda Iye kwa muyaya. Anthuwa amene ayenera kulamulilidwa ndi Mulungu adzasangalala muchikondwerero chao. Ndipo cifukwa cha chisangalalochi, iwo adzapereka ulemerero kwa mkwati. 

Anthu onse akhala ali kudikhira za cimenechi kuchokera pa kulenga kwa dziko. Ichi chidzakwalitsidwa ngati Yesu abweranso, n’kutenga onse amene analandira Mzimu Woyera, ndi wukhala ndi iwo. Mulungu analenga dziko la tsopano la anthu ndipo likudikhira ife. Tikhalapo cifukwa cha ichi, ndipo cifukwa cha ichi tinabwa mdzikoli lapansi. 

Monga mmene ndime yomwe tawerenga imatiuzira, “ndipo mkazi wake wadzikongoletsa Iye waloledwa kuvala zovala zapamwamba, zonyezimira ndi zoyera bwino,” Mulungu wabvalika onse amene okhulupilira mwa Yesu Khristu mu zobvala zoyera bwino, zapamwamba zonyezimira. Onse amene okhulupilira mu Mawuwa, mmawu ena, analandira chikhululuko cha uchimo ndipo mitima yawo yasanduka yoyera ngati matalala. 

Monga ichi, akwatibwi a Yesu Khristu ndi okodzekera kale nthawi isanafike ndi uthenga wa madzi ndi Mzimu. Pomvetsera ndi kukhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu pamene okhalabe padzikoli lapansi, wina angabadwe mwatsopano ngati mkwatibwi wa Yesu Khristu. Chikhulupilirochi ndi cimene chimakupangani inu kukhala akwatibwi a Yesu Khristu, ndipo chikhulupilirochi ndi cimene chimakwalitsa kuti inu mulowe Kumwamba. Onse Amene Adikhira mu Chiyembekezo 


Ndime yomwe tawerenga imatiuza kuti, “Odala ndiwo amene aitanidwa ku phwando la chakudya chamadzulo la ukwati wa Mwanawankhosa!” Kodi ndi mtundu oitani wa chikhulupiliro cymene onse amene analandira chikhululukiro cha machimo awo ayenera kukhala? Akwatibwi amene anakumana ndi Mkwati wawo Yesu ndipo okhala mu ulemerero ayenera kukhala miyoyo yawo mchikhulupiliro ndiponso mchiyembekezo, kumapenya kutsogolo za tsiku limene adzakhala limodzi ndi Mkwatiyu. 

Monga mmene dziko lapansi lili kukhala la mdima mdima, komabe chiyembekezo chilipo cha akwatibwi opulumutsidwa, chiyembekezochi ndi kudikhira kwa tsiku limene Yesu, anakonza Kumwamba kwa Tsopano ndiponso Dziko lapansi la akwatibwi Ake, adzabweranso kuti awatenge. Ndiyeno Mkwati adzaukitsa akwatibwi Ake onse, ndi kuwapatsa iwo moyo wosatha. Dziko limene Mkwati ndi akwatibwi adzakhalamo kwa muyaya ndi dziko limene lilibe zoipa, lilibe uchimo, ndipo palibe cimene likusowekera. Akwatibwi akudikhira za tsikuli lokha. Ichi ndicho cifukwka onse amene analandira chikhululukiro cha machimo athu onse okhala ndi chikhulupiliro ndi chiyembekezo chotero. 

Akwatibwi amene tsopano ali kukhala mnthawi ino, makamaka, naonso ali ndi zolakwika zathupi zambiri. Koma monga mmene 1 Akorintho 13:13 imatiuzira, “Komabe, tsopano patsala zitatu izi: Chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi. Koma chachikulu pa zonsezi ndi chikondi,” cifukwa Mkwati ndimmene anakondera akwatibwi Ake, Iye adzasuka machimo awo onse ndi ubatizo Wake ndipo Iye anawamvomera iwo ngati akwatibwi Ake angwiro. 

Dzikoli likuthawira kuchionongeko chake chomaliza ndipo mulibenso chiyembekezo chotsiyidwa mmenemo. Koma ngakhale zinthu zonse zikuthawira kufupi ndi chionongeko, akwatibwi ayenera kukhala miyoyo yawo ndi chiyembekezo chao chapatulika. Nthiwa yokwanilitsira chiyembekezochi tsopano ili kufenderera pafupi ndi ife. Tsopano dziko lonse lili pa chiopsezo cha kugwa ndi zovomezi. Tsiku lafenderera pafupi ndi wina aliyense mdzikoli lapansi azimiririke ngati madinoza a mthawi ya kale. Mwadzizizi, dzikoli lidzagwa.

Mkwabwi wina aliyense, chonchi, ali ndi chiyembekezo, cifukwa ngati nthawi yabwera, mathupi a akwatibwi adzasandulitsidwa mmathupi angwiro, ndipo iwo adzakhala ndi Ambuye, amene wakhala mkwati wao, kwa muyaya. Akwatibwi, choncho, ayenera kulalikira uthenga wa madzi ndi Mzimu mokhulupirika kwambiri ku anthu a nthawi ino. Tiyeni Tikhulupilire mu Mawu Oona a Mulungu! 


Yesu amatiuza mu Yohane 3:5, “Yesu anayankha kuti: Ndithudi ndikukuuza, Munthu sangathe kulowa mu ufumu wa Mulungu atapanda kubadwa mwa madzi ndi mzimu.” Kodi, ndiyeno, uthenga wa madzi ndi Mzimu n’ciani? Baibulo limatiuza, poyamba pa zonse, kuti “madzi” poyerayera aimilira ubatizo wa Yesu, ndipo n’chifaniziro cha chipulumutso (1 Petulo 3:21). 

Pamene Yesu anafika zaka 30, Iye anapita kwa Yohane, amene anakhala ali kubatiza anthu a Israeli mu Mtsinje wa Yordani. Yesu anauza Yohane M’batizi amene anali oimililako anthu ndipo Wansembe Wamkulu womaliza wa mu Pangano la Kale. Kukumana ndi Yohaneyu, Yeus analandigra ubatizo Wake kuchokera kwa iye, umene unakwanilitsa chilungamo chonse cha Mulungu (Mateyu 3:15, 11:11-14). Ubatizo umene Yesu analandira unali chopereka chosatha kupyolera mu cimenechi machimo onse adziko lapansi inaikidwa pa Khristu Iyeyekha. 

Kubadwa kwa Yesu kupyolera mu Mzimu Woyera, ubatizo Wake, magazi Ake ndi imfa pa Mtanda, ndiponso kuukitsidwa ndi kukwera Kwake—zonse zinthuzi zinali ntchito za Mzimu Woyera. Ngati wina okhulupilira kuti Yesu anabwera padzikoli lapansi ndipo anapanga, kupyolera mu madzi ndi Mzimu, kuti machimo ake azimiririke kamodzi kokha, kotero kuti ndiyeno iye akhala munthu olungama, omasuka kuchoka ku uchimo, ndipo akhale mkwatibwi wa Khristu. Ichi sichinthu chokwanilitsidwe ndi maganizo a munthu, koma chimochoka ku maganizo a Mulungu Iyeyekha. 

Choonadi ndi chakuti madzi, magazi, ndiponso Mzimu Woyera ndi zinthu zitatu zofunikira pa chipulumutso cha anthu kuchoka ku uchimo, ndipo palibe chimodzi cha izi cimene chingachotsedwapo mwina mulimonse. Baibulo limanena mozama pa zaichi bwino bwino ndipo moona mu chapitala 5 ya 1 Yohane. Imatiuza kuti zinthuzi zitatu madzi, magazi, ndipo Mzimu Woyera zonse n’zimodzi, ndi kuti chipulumutso chathu kuchoka ku uchimo sichingakhale chofikapo ndiponso chololedwa ngati chimodzi cha izo sichipezekapo. 

Ngati tudziwa ndi kukhulupilira mu choonadichi, kuti chipulumutso cha ngwiro ndi kukhulupilira mu zinthuzi zitatu—madzi, magazi, ndiponso Mzimu Woyera—ndiyeno tingadzindikire ndi kumvomera chikondi cha Yesu kuti anatipulumutsa ife, ndipo ndimene mitima yathu ingakhaledi yopanda uchimo. Baibulo limatilonjeza mu Machitidwe 2:38, “Lapani, m ndipo aliyense wa inu abatizidwe m’dzinao la Yesu Khristu kuti machimo anu akhululukidwe. Mukatero mudzalandira mphatso yaulere ya mzimu woyera.” 

Kodi, ndiyeno, ndi Mawu otaniwa amene amalora kuti ife tilandire Mzimu Woyera? Awa ndiwo Mawu a ubatizo wa Yesu (madzi), a imfa Yake pa Mtanda (magazi), ndipo a kukhala Mulungu Kwake, chiukitso ndiponso kukwera (Mzimu Woyera). Mawuwa a chipuluutso analotseredwadi mu malemba a Mose ndi aneneri ena a mu Pangano la Kale, ndipo anakwanilitsidwa ndi kuchitilidwa umboni mu Mauthenga anayi a mu Pangano la Tsopano. Ndiponso, “chipulumutso chosatha cha chikululuko chinakwanilitsidwa kamodzi kokha,” chimene chinalembedwa mozama mu Buku la Aheberi, mobwerezabwereza limachitira umboni wa chilungamo cha Mulungu, chimene tinalanndira kupitila muchikhulupiliro. 

Ngakhale wina aliyense mdzikoli la uchimo okhala moyo wa thupi umene uperewera pamaso pa Mulungu, iye ayenera kulandira chikhululukiro cha uchimo chopatsidwa ndi Mulungu, ndipo wina akhale moyo wake poika chiyembekezo chake Kumwamba. Ili ndi dalitso la Mulungu limene Iye anali pereka ku anthu. Tonse tiyenera kuchilandira chisomocho chopatsidwa kwa ife mwaulele. Kukhulupilira mu Mawu akuti Ambuye athu adzabweranso, kudzamanga Ufumu Wake, ndi kutilora kukhala mu umenewo n’chiyembekezo chatu choona. Tiyenera kukhala nbdi chiyembekezochi, ndipo ichi ndi cimene Ndikhulupilira kwambiri.

Kodi inu mkudziwa mmene uchimo wafalikira mdzikoli lapansi? Kuyerekeza ndi nthawi ya kusefuki kwa madzi ya Nowa, machimo a nthawi iuno afalikira kwambiri. Mnthawi ya Nowa, ataona kuti maganizo a munthu tsiku ndi tsiku anali oipa, Mulungu anaganiza kuononga dziko loyamba ndi kusefukira kwa madzi, anauza Nowa kuti apange ngalawa, ndi kupulumutso onse amene analowa mu ngalawayi pokhulupilira mu Mawu Ake.

Ngakhale kuti Mulungu anati Iye adzaweruza dziko ndi madzi, ndi banja la Nowa lokha la anthu 8 anakhulupilira mu Mawu Ake. Ndicho cifukwa anapanga ngalawa kwa nthawi yopililira pa zaka-zana limodzi, ndipo analowamo kuthawa kusefukira kwa madzi. Pamene anachita tero, Mulungu anayamba kubweretsa chiweruzo Chake padziko loyamba. Mtambo unasanduka mdima mwadzizizi, ndipo mvula ya matalala inayamba kugwa. Mwadzizizi mu kanthawi ka ola limodzi kokha, madzi anafika kale pambwamba ngati pa mtenge wa chitatu. Choncho inagwa kwa matsiku 40, kumbilitsa dziko lonse lapansi mmadzi. 

Monga mmene Nowa ndi banja lake analowera mungalawa kukhukupilira kuti dziko la tsopano lilipafupi kutseguka, inu ndi Ine tiyenera kukhala mnthawi ino muchiyembekezo. Monga mmene iwo anakwanitsa kumanga ngalawa kwa zaka zana limodzi cifukwa iwo anakhulupilira mwa Mulungu, Ine n’khulupilira kuti ife, nasenso, tiyenera kupilira ndi kulalikira uthenga. Mulungu anauza Nowa, “udzipangire chingalawa (Genesis 6:14).” Mawuwa amatiuza kuti ‘ife titeteze chikhulupiliro chathu,’ poyamba tiyenera kudzipereka ife tokha kwa Ambuye ndi kulalika uthenga. 

Ngakhale kuti obadwa-mwatsopano ali n’chiyembekezo, kulibe chiyembekezo cha onse amene sakhulupilira mu uthenga. Kuli chionongeko choka cha osakhulupilirawa a uthenga. Kosaganizira za kuti mwina anthuwa okhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu kapena ai, tiyenera kuulalikirabe ku iwo mwa chikhulupiliro. Nthawi ino ndi mtundu wa nthawi imene anthu ayenera kukhulupilira mu uthengawu oona mwamsanga mmene angakwanitsire. Onse amene okhulupilira mu uthenga umene timalalikira adzapeza chikondwerero, koma onse amene sakhulupilira mu umenewu adzatembereredwa chabe. Omaliza—amene ndi, onse amene sakhulupilira mu uthenga—ndi azitsiru amene adzalandira chiweruzo cha Mulungu chosatha ndipo adzaponyedwa mgehena. 

Musataye chiyembekezo chanu. Ngati olungama akanataya chikulupiliro chao, ndi imfa yokha imene ikuwadikhira iwo. Ngati tilibe chiyembekezo, tikanakhala mwina tilibe funiro, kapena chidwi, kapena funiro lilonse lokhala moyo. Tiyeni, choncho, tikhale ndi chiyembekezo. 

Mnthawi ino, onse amene akhulupilira mwa Yesu ndipo choncho anabadwa mwatsopano ndi okondweradi. Ku anthu, ndi chiyembekezo chokha chimene chinatsala kuti alandire chikululukiro cha uchimo—cimene ndi, kulibe chiyembekezo china chilichonse koma kulandira Mzimu Woyera. Ngati anthu akhululukidwa machimo awo onse, angakhale ndi chiyembekezo ndiponso kukhala okondwera kwa muyaya, koma ngati alibe, n’chionongeko chokha cimene cidzwadikhira iwo, cifukwa iwo sanalandire Mzimu Woyera. 

Ndi cifukwa chakuti Ndinalandira chikhulukiro cha machimo anga onse, kotero Ndingakhale mdzikoli la matsiku ano ndi chiyembekezo. Ndi chiyembekezo changa ndiponso pemphero langa kuti inu, nanunso, mkhale miyoyo yanu ndi chiyembekezochi. Ndipemphera kuti inu msadzigumanye ku maganizo opanda pache adziko lapansi, mmalo mwake khalani miyoyo yanu ngati mkwatibwi wa nzeru, okonda abale ndi alongo anu olungama, kuwathandiza kuti aime njii mwa Khristu, kosataya chikhulupiliro chanu, kudikhira Mkwati, ndipo kukumana ndi Iye ngati abwera Iye kudzakutengani.

Ndithokoza Mulungu potilora kuti tikhale mu ulemerero Wake.