Sermons

[20-1] < Chivumbulutso 20:1-15 > Chinjoka Chidzathiridwa Unyolo Pa Dzenje Lolowera Paphompho< Chivumbulutso 20:1-15 >

“Ndipo ndinaona mngelo akutsika kuchokera kumwamba ali ndi kiyi wa paphompho ndi unyolo waukulu m’dzanja lake. Kenako anagwira chinjoka, njoka yakale ija, amene ndi Mdyerekezi ndiponso Satana, ndi kumumanga zaka 1,000. Ndipo anamuponyera m’phompho ndi kutseka pakhomo pa phompholo n’kuikapo chidindo kuti asasocheretsenso mitundu ya anthu kufikira zitatha zaka 1,000. Pambuyo pake, adzamasulidwa kanthawi kochepa. Kenako ndinaona mipando yachifumu ndi amene anakhalapo. Iwo anapatsidwa mphamvu yoweruza. Ndiyeno ndinaona miyoyo ya amene anaphedwa ndi nkhwangwa chifukwa cha kuchitira umboni za Yesu, ndi kulankhula za Mulungu. Ndinaonanso anthu amene sanalambire chilombo kapena chifaniziro chake, ndipo sanalandire chizindikiro pamphumi pawo ndi padzanja pawo. Iwo anakhalanso ndi moyo ndipo analamulira monga mafumu limodzi ndi Khristu zaka 1,000. (Akufa enawo sanakhalenso ndi moyo kufikira zitatha zaka 1,000.) Uku ndi kuuka koyamba kwa akufa. Wodala ndi woyera ndiye aliyense wouka nawo pa kuuka koyamba. Pa iwo, imfa yachiwiri ilibe ulamuliro. Koma adzakhala ansembet a Mulungu ndi a Khristu, ndipo adzalamulira monga mafumu limodzi naye zaka 1,000. Tsopano zikadzangotha zaka 1,000, Satana adzamasulidwa m’ndende yake, ndipo adzatuluka kukasocheretsa mitundu ya anthu kumakona onse anayi a dziko lapansi. Mitunduyo ndiyo Gogi ndi Magogi, ndipo adzaisonkhanitsa pamodzi kunkhondo. Kuchuluka kwawo kudzakhala ngati mchenga wa kunyanja. Iwo adzayenda n’kufalikira mpaka kumbali zonse za dziko lapansi, kenako adzazungulira msasa wa oyera, a ndi mzinda wokondedwa.

Koma moto udzatsika kuchokera kumwamba ndi kuwapsereza. Mdyerekezi, amene anali kuwasocheretsa, adzaponyedwa m’nyanja yamoto ndi sulufule, mmene muli kale chilomboe ndi mneneri wonyenga uja. Ndipo iwo adzazunzidwa usana ndi usiku kwamuyaya. Kenako ndinaona mpando wachifumu waukulu woyera, ndi amene anakhalapo. Dziko lapansi ndi kumwamba zinathawa pamaso pake, ndipo malo a zimenezi sanapezekenso. Ndiye ndinaona akufa, olemekezeka ndi onyozeka, ataimirira pamaso pa mpando wachifumuwo, ndipo mipukutu inafunyululidwa. Koma mpukutu wina unafunyululidwa, ndiwo mpukutu wa moyo. Ndipo akufa anaweruzidwa malinga ndi zolembedwa m’mipukutuyo, mogwirizana ndi ntchito zawo. Nyanja inapereka akufa amene anali mmenemo. Nayonso imfa ndiManda zinapereka akufa amene anali mmenemo. Aliyense wa iwo anaweruzidwamalinga ndi ntchito zake. Ndipo imfa ndi Manda zinaponyedwa m’nyanja yamoto. Nyanja yamoto imeneyi ikuimira imfa yachiwiri. Komanso, aliyense amene sanapezeke atalembedwa m’buku la moyo anaponyedwa m’nyanja yamoto.” Kusanthula


Ndime ya 1: Ndipo ndinaona mngelo akutsika kuchokera kumwamba ali ndi kiyi wa paphompho ndi unyolo waukulu m’dzanja lake.

Kuti awalipile oyera amene atumikira uthenga ndi mphoto Zake, Ambuye Mulungu wathu adzawapatsa mphatso ya Ufumu wa Khristu kwa zaka 1000. Kuti achite tero, Mulungu ayenera kuuza umodzi wa Angelo Ake kuti agwire Chinjoka ndi kumuika m’ndende paphompho kwa zaka 1000. Mulungu ayenera kuchita ntchotoyi poyamba, cifukwa Chinjoka chiyenera kugwiridwa ndi kuthiridwa unyolo Paphompho nthawi isanafike kuti alore oyera kukhala mu Ufumu wa zaka Chikwi chimodzi wa Khristu. Mulungu chonchi apereka kiyi wa dzenje lolowera kuphompho ndi unyolo waukulu, ndikumuuza iye kuti ayambe ntchito yogwira ndi kuthiri unyolu Chinjoka Paphompho. 


Ndime ya 2: Kenako anagwira chinjoka, njoka yakale, amene ndi Mdyerekezi ndiponso Satana, ndi kumumanga zaka 1,000; 

Amene anayetsa ndiponso kupanga Adamu ndi Hava agwe ndi njoka yakale imene. Baibulo limatchula njokayi Mdyerekezi ndiponso Satana. Mulungu adzagwira Mdyerekeziyu ndi kumumanga paphompho kwa zaka 1000, kotero kuti oyera adzakhala ndi Khristu mu Ufumu wa zaka Chikwi chimodzi mmtendere. 


Ndime ya 3: Ndipo anamuponyera m’phompho ndi kutseka pakhomo pa phompholo n’kuikapo chidindo kuti asasocheretsenso mitundu ya anthu kufikira zitatha zaka 1,000. Pambuyo pake, adzamasulidwa kanthawi kochepa. 

Kotero kuti amange Ufumu wa Khristu padzikoli lapansi ndi kupanga oyera kuti alamulire limodzi ndi Ambuye kwa zaka 1000, Mulungu adzathira unyolo Chinjoka paphompho kwa zaka 1000, ndi kumuchingamira iye kuchoka kukusocheretsa oyera. 

Ndime apa ikuti, “Pambuyo pake, adzamasulidwa kanthawi kochepa.” Ngati zaka 1000 zapita, Mulungu adzachimasula Chinjoka kwa kanthawi kochepa, kotero kuti ngati aayambanso kuzunza oyera, Iye ndiyeno adzamupereka iye mgehena kwa muyaya, sadzaonekanso. 


Ndime ya 4: Kenako ndinaona mipando yachifumu ndi amene anakhalapo. Iwo anapatsidwa mphamvu yoweruza. Ndiyeno ndinaona miyoyo ya amene anaphedwa ndi nkhwangwa chifukwa cha kuchitira umboni za Yesu, ndi kulankhula za Mulungu. Ndinaonanso anthu amene sanalambire chilombo kapena chifaniziro chake, ndipo sanalandire chizindikiro pamphumi pawo ndi padzanja pawo. Iwo anakhalanso ndi moyo ndipo analamulira monga mafumu limodzi ndi Khristu zaka 1,000. 

Mu Ufumu wa Khristu, Akristu obadwa-mwatsopano adzalandira ulamuliro oweruza. Oyera, atasandalidwa kukhala ansembe a Khristu, adzalamulira Ufumu wa zaka Chikwi chimodzi ndi Ambuye. Okhalamo ake ndi aja anaphedwa pochitira umboni wa Yesu ndipo poteteza chikhulupiliro chao, amene sanalandire chidzindikiro cha Chilombo kapena kulambira chifaniziro chake. 

Iwo ndi amene anaphedwa mnthawi ya masautso obweretsedwa ndi Wosusa Khristu, ndipo Mulungu adzawaukitsa iwo kukhalanso moyo ndi kulamulira mu Ufumu wa Khristu kwa zaka 1000 zikubwera. Ndithudi, onse amene adzatengako mbali muchiukitso choyamba naonso adzapatsidwa dalitso limodzimodzi. 

Pali kuukitsidwa kuwairi kopatsidwa ndi Ambuye: Chiukitso choyamba ndiponso chiukitso chachiwiri. Oyera amene adzakhala mu Ufumu wa zaka Chikwi chimodzi ndi amene adzakhala ndi kutengako mbali mu chiukitso choyamba. Onse amene a adzatengako mbali mu chiukitso choyambacho adzatengekonso mbali mu ulemerero okhala mu Ufumu wa zaka Chikwi chimodzi, mu Ufumu wa Khristu. Chiukitso choyamba chidzachitika pamene Yesu Khristu adzabweretsa kudzakwatula oyera onse (1 Atesalonika 4:15-17). Koma chachiwiri chidzachitika pomaliza Ufumu wa zaka chikwi chimodzi cifukwa chinakonzedwera ochimwa amene kuti awagamulire ku imfa yosatha. 

Ulamuliro wa oyera oalmulira kwa zaka 1000 udzapatsidwa ndi Ambuye Wamphamvuyonse. Ufumu wa Khristu udzapatsidwa kwa iwo cifukwa iwo anakhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu wa Ambuye ndipo anapereka miyoyo yawo kuti ateteze chikhulupiliro chao. 


Ndime ya 5:5 (Akufa enawo sanakhalenso ndi moyo kufikira zitatha zaka 1,000.) Uku ndi kuuka koyamba kwaakufa. 

Onse amene, sanalandire chikhululukiro cha machismo awo kuchokera kwa Ambuye, kupita kwa Iye pambuyo pokhala pdzikoli lapansi ngati ochimwa sadzakwanitsa kutengeko mbali muchiukitso choyamba cymene Ambuye adzapereka ku oyera. Choncho, ngakhale pamene oyera adzakhala kwa zaka 1000 mu Ufumu wa Khristu mu phwando, iwo sadzalandira chiukitso choyamba, koma iwo mmalo mwake adzatengeko mbali mu chiukitso cha chachiwiri. Cifukwa n’chakuti oyera amene adzalandira dalitso la chiukitso choyamba adzalandiranso ulamuliro okhala mu Ufumu wa Khristu, mchuma ndiponso mu ulemerero, kwa zaka 1000. 

Ngakhale tero, Mulungu adzalora “chiukitso cha chiwiri” ku ochimwa. Cifukwa n’ciani? Cifukwa pa nthawi ya chiukitso choyamba, Mulungu adzawaukitso kuchokera ku imfa kotro kuti Iye awaweruze cifukwa cha machimo awo. Chigamulo chao n’chakuti iwo ayenera kuukitsidwenso kuchoka ku akufa kuti aweruzidwa cifukwa cha machimo awo. Ichi ndicho cifukwa chiukitso cha oichimwa chimatsiya ndi cha oyera monse mndondomeko ndiponso mdzotulukamo. 

Kuchotsako amene adzatengako mbali mu chiukitso choyamba cifukwa cha chikhulupiliro chao mu uthenga wa madzi ndi Mzimu, Ambuye sadzalora wina aliyense kukhalanso moyo kufikira zitatha zaka 1000. Choncho, chiukitso cha olungama chidzakhalako zaka 1000 chiukitso cha ochimwa chisanafike. Chiukitso cha olungama n’chakuti iwo alanndire moyo osatha ndi madalitso, koma chiukitso cha ochimwa ndi n’chakuti iwo alandire chilango chosatha cifukwa cha machimo awo. 


Ndime ya 6: Wodala ndi woyera ndiye aliyense wouka nawo pa kuuka koyamba. Pa iwo, imfa yachiwiri ilibe ulamuliro. Koma adzakhala ansembet a Mulungu ndi a Khristu, ndipo adzalamulira monga mafumu limodzi naye zaka 1,000. 

Baibulo imatiuza kuti imfa ya chiwiri ilibe mphamvu pa onse amene adzatengako mbali mu chiukitso choyamba. Choncho, imatiuza kuti otengako mbaliwa a mu chiukitso choyamba ndi odala, cifukwa iwo adzalamulilanso mu Ufumu wa zala Chikwi chimodzi. 


Ndime ya 7-8: Tsopano zikadzangotha zaka 1,000, Satanaadzamasulidwa m’ndende yake, ndipo adzatuluka kukasoc-heretsa mitundu ya anthu kumakona onse anayi a dziko lapansi. Mitunduyo ndiyo Gogi ndi Magogi, ndipo aadzaisonkhanitsa pamodzi kunkhondo. Kuchuluka kwawo kudzakhala ngati mchenga wa kunyanja.

Adzamasulidwa pambuyo potsekeredwa paphompho kwa zaka 1000, Chinjoka chifunaso kususana ndi oyera, ndipo chotero Mulungu adzamuponya iye mmoto wa sulufule kotero kuti iye sadzakwanitsa kuchokeranso kunja. Ndi chiweruzochi, Chinjoka chidzaoneka mgehena mocha.

Ndiyeno mwina tingafunse, “Kodi ichi chitanthauza kuti onse amene sanabawe mwatsopano adzakhalabe moyo mu Ufumuwu wa zaka chikwi chimodzi?” Yankho ndi, “Inde.” Chivumbulutso 20:8 munalembedwa kuti muli anthu ambiri mu Ufumu wa Khristu. Si tikudziwa mchoona mwina iwo ndi anthu olengedwa tsopano ndi Mulungu, kapena ndi amene anakhalapo kumbuyo padzikoli lapansi. Koma cimene tikudziwa n’chakuti Mulungu akudziwa amene ndi anthuwa, ndipo kuti oyera alamulire, kudzakhala khamu lalikulu la iwo, kuchuluka kwao ngati mchenga wa kunyanja. 

Choona ndi chakuti ngati oyera okhala mu Ufumu wa Khristu, iwo adzaonabe anthu a adziko lapansi. Iwo adzakhalapo kutumikira oyera, ndipo nambala yawo idzachuluka ngati mchenga wa kunyanja. Ngakhale kuti adzazisonkhanitsa ndi Chinjoka kususananso ndi oyera, onse adzaonongedwa ndi moto obweretsedwa ndi Mulungu, adzalandira chiweruzo chosatha cha mpando Wake oyera wachifumu, ndipo adzaponyedwa mmoto woyaka kwa muyaya. Ndi cimenechi, Ufumu wa zaka Chikwi chimodzi udzatsekedwa, ndipo kuchokera pomwepo oyera adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba ndiponso Dziko lapansi mmene adzakhala kwa muyaya. 

 

Ndime ya 9: Iwo adzayenda n’kufalikira mpaka kumbali zonse za dziko lapansi, kenako adzazungulira msasa wa oyera, a ndi mzinda wokondedwa.Koma moto udzatsika kuchokera kumwamba ndi kuwapsereza. 

Chinjoka ndi Satana amene akhala ali kususana ndi Mulungu kosalekeza ndi oyera Ake. Ngakhale kuti iye angasocheretse anthu adziko lapansi okhala mu Ufumu wa Khristu ndi kuopseza oyera, cifukwa Mulungu ndi wamphamvuyonse, Iye adzabweretsa moto kuchokera mmtambo ndi kuwaotcha onse aiwo, ndi kuponya Chinjoka mmoto wosatha kuti chisasusanenso ndi Iye ndiponso oyera Ake.


Ndime ya 10: Mdyerekezi, amene anali kuwasocheretsa, adzaponyedwa m’nyanja yamoto ndi sulufule, mmene muli kale chilomboe ndi mneneri wonyenga uja. Ndipo iwo adzazunzidwa usana ndi usiku kwamuyaya. 

Poponya Mdyerekezi m’nyanja yamoto ndi sulufule, Mulungu adzaonetsetsa kuti iye akuzunzidwa usana ndi utsiku. Ichi ndin chiweruzo cholungama cha Mulungu, kuzunzidwa kumene Mdyerekezi ndi omusatira ake n’chowayenerera. 


Ndime ya 11: Kenako ndinaona mpando wachifumu waukulu woyera, ndi amene anakhalapo. Dziko lapansi ndi kumwamba zinathawa pamaso pake, ndipo malo a zimenezi sanapezekenso.

Atatsiriza kuwapatsa mphoto oyera kwa zaka 1000, tsopano Mulungu adzalengenga Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi ndi kukhala mmalowa ndi iwo kwa muyaya. Kuti akwanilitse ichi, Mulungu adzabweretsa ntchito zonse zimene Iye anachita kuti zitsirizitsidwe ndi kudzitseka, kuchita komaliza, kwa kutseka, ndi kwa Ambuye kuti akhale pampando wachifumu oyera monga Oweruza ndi kupereka chiweruzo Chake chomalizira pa ochimwa onse, amene zochita zake zinalembedwa mu Buku la Zochita, kuchotsako onse amene maina awo analembedwa mu Buku la Moyo. 

Chiweruzo cha Mulungu cha ochimwa chidzamaliza ndi ichi, ndnipo kuchokera pamenepo malo a Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi adzatseguka. Ambuye athu adzapanga kumwamba koyamba ndi dziko lapansi loyamba kuzimiririka, n’kulenga dziko lachiwiri la Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi, ndi kulora oyera kukhala mu Ufumuwu wa kumwamba. Kulingana ndi zimene zinalembedwa mu Buku Lake la Moyo ndiponso mu Mabuku a Chiweruzo, Mulungu adzapereka Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi ku gulu lina la anthu, ndiponso chilango cha gehena ku lina. 


Ndime ya 12: Ndiye ndinaona akufa, olemekezeka ndi onyozeka, ataimirira pamaso pa mpando wachifumuwo, ndipo mipukutu inafunyululidwa. Koma mpukutu wina unafunyululidwa, ndiwo mpukutu wa moyo. Ndipo akufa anaweruzidwa malinga ndi zolembedwa m’mipukutuyo, mogwirizana ndi ntchito zawo.

Chiweruzo cha Khristu pa nthawiyi chidzatengera chiweruzo chomaliza—cimene ndi, Iye adzapereka chigamula chomaliza pa ochimwa ndi chilango cha gehena. Adzaweruzidwa kulingana ndi ntchito zawo, monga mmene zinalembedwera mu Buku la Chiweruzo. Ochimwa ndimmene adzafa kawiri. Imfa yachiwiri ndi kuzunzidwa mgehena, imene Baibulo imasulira ngati imfa yosatha. Ochimwa sangathawe kuchoka ku chilango cha gehena. Iwo, choncho, ayenera kufuna funa kuphunzira Mawu a uthenga wa madzi ndi Mzimu tsopanopa, pamene ali kukhalabe padzikoli lapansi, akhulupilire mmenemo, ndipo ndiyeno alandire dalitso la maina awo kulembedwa mu Buku la Moyo.


Ndime ya 13: Nyanja inapereka akufa amene anali mmenemo. Nayonso imfa ndiManda zinapereka akufa amene anali mmenemo. Aliyense wa iwo anaweruzidwa malinga ndi ntchito zake. 

“Nyanja inapereka akufa amene anali mmenemo.Nayonso imfa ndi Manda zinapereka akufa amene anali mmenemo,” cifukwa ochimwa onse ayenera kulandira kusutsidwa komaliza cifukwa cha machimo awo. Malo amene atchulidwa mndimeyi imfa ndi manda, amene—makamaka aimilira malo amene atumiki a Satana amene, anasocheretsedwa ndi iye ndipo kukhala pansi pa ulamiliro wake pamene ali moyo, anasusana ndi kumuchimwira Mulungu adzathiridwa unyolo. Ndimeyi imatiuza kuti pamene Mulungu adzangeleza kubweretsa chiweruzo Chake cha machimo awo kwa kanthawi kochepa, tsopano nthawi yabwera ya chiweruzo chao chomaliza. 

Choncho, kulikonse kumene anthu angakhale, ayenera kudzindikira kuti ku amene iwo odzipereka ndi kofunikira kwambiri. Onse amene akhala ali kugwira ntchito ngati atumiki a Satana pamene anali padzikoli lapansi adzaukitsidwa kuchoka ku akufa ndi chiukitso cha chilango kuti alandire chiweruzo chao chomaliza, koma onse amene anatumikira uthenga wa madzi ndi Mzimu ndi a chiukitso cha umoyo ndi madalitso osatha.

Choncho, anthu ayenera kudzindikira pamene okhala padzikoli lapansi kuti uthenga wa madzi ndi Mzimu, ndi umene Ambuye anafafanizira machimo a anthu onse, ndi ofunikira kwambiri. Onse amene akhala ali kugwira ntchito ngati atumiki a Satana padzikoli lapansi adzaukitsidwa ndi chiukitso cha chilango, koma onse amene akhala ali kutumikira ntchito za chilungamo cha Ambuye athu adzaukitsidwa ndi chiukitso cha moyo ndi madalitso osatha. Ochimwa onse adzaweruzidwa cifukwa cha zolakwa zawo ndipo adzalandira chiweruzo chao chomaliza mgehena. Ndi pamenepa pomwe timapeza cifukwa chenicheni cha cifukwa chomwe tiyenera, pamene tili kukhala padzikoli lapansi, anakhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu, uthenga ndiumenewo Ambuye anachotsera machimo athu onse. 


Ndime ya 14: Ndipo imfa ndi Manda zinaponyedwa m’nyanja yamoto. Nyanja yamoto imeneyi ikuimira imfa yachiwiri. 

Ichi chimatiuza za chiweruzo cha machimo a anthu onse pamaso pa Mulungu, amene anachita poimilira kumbali ya Satana. Chilango cimene chinasungidwira oipa amene anatsogolera anthu kwa Satana ndi kuponyedwa m’nyanja yamoto. Iyi ndi imfa yachiwiri imene Mulungu adzabweretsa ku ochimwa, ndipo ndi chilango cha m’nyanja yamoto. Imfa imene Baibulo limalankhula apa si kuzimiririka kokha, koma ndi chilango cha kuzunzidwa kosatha mgehena oyaka moto. 

Chipulumutso cholankhulidwa ndi Malemba si cha nthawi yochepa, koma, chosatha. Onse amene okhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu pamene ali mdzikoli lapansi adzalowa mu Ufumu wosatha wa Kumwamba ndipo adzakhala mokondwera kwa muyaya. Kutsiyana pakati pa mphoto ya okhulupilira a uthenga wa madzi ndi Mzimu ndi chilango cha osakhulupilira ndi kutsiyana kwakukulu ngati pakati pa Kumwamba ndi Dziko lapansi. 


Ndime ya 15: Komanso, aliyense amene sanapezeke atalembedwa m’buku la moyo anaponyedwa m’nyanja yamoto.

Ndi mawu akuti “aliyense” apa, ndimeyi imatiuza kuti mwina kapena ai maina a anthu amalembedwa mu Buku la Moyo chiimilira makamaka pa mwina iwo okhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu, kupitira mu umene machimo awo onse amakhululukidwa, kuyera mbee ngati matalala, kosaganizira kuti mwina iwo ndi odziwa bwino-kumapita kuchalichi, kapena mwina machilichi awo ndi amipingo ya arthodox kapena heterodox. Onse amene maina awo analembedwa mu Buku la Moyo la Ambuye, choncho, onse adzaponyedwa m’nyanja yamoto kopanda kukondera. 

Anthu azipembezo za dziko lapansi ali ndi mkhalidwe odziwika bwino oika nzeru kwambiri mu miyambo ya zipembezo zawo koposa muchiombolo kuchoka ku uchimo. Koma ngati taima pamaso pa Mulungu, ngati uthenga wa madzi ndi Mzimu wopatsidwa ndi Yesu supezeka mmtima wa wina, dzina la munthuyu silidzapezeka mu Buku la Moyo, ndipo iye ndimene nayenso adzaponyedwa m’nyanja yamoto, ngakhale kuti wina anali Mkristu wabwino bwino. 

Choncho, pamene inu muli kukhalabe padzikoli lapansi, muyenera kumva ndi matu anu uthenga wa Ambuye wa madzi ndi Mzimu umene unapanga machimo anu onse kuzimiririka, ndipo muyenera kukhulupilira mu umenewo ndi mtima wanu wonse. Ndiyeno mdzalandira ulemerero olembedwa dzina lanu mu Buku la Moyo.