Sermons

[20-2] < Chivumbulutso 20:1-15 > Kodi Tingapite Motani Kuchoka ku Imfa Kupita ku Moyo?< Chivumbulutso 20:1-15 >


Mulungu amatiuza kuti ngati Iye apanga dzikoli kizimiririka ndi kutipatsa Kumwamba kwa Tsopano ndiponso Dziko lapansi mmalo mwake, iye adzaukitso ochimwa aliyense amene anakhalapo padzikoli lapansi ndipo iye akhala ali kugona mmanda ake. Ndime ya 13 apa ikuti, “Nyanja inapereka akufa amene anali mmenemo. Nayonso imfa ndiManda zinapereka akufa amene anali mmenemo. Aliyense wa iwo anaweruzidwa malinga ndi ntchito zake.” Thupi la munthu amene ambira mmadzi aliyense adzadwedwa ndi nsomba, pamenethupi la munthu amene aotchedwa mpaka kufa adzakhala opanda moonekedwe kuti adzindikilidwenso. Koma Baibuo apa limatiuza kuti ngati nthawi zomaliza zabwera, Mulungu adzaukitsa onse kubwerera ku moyo ndi kuwaweruza kotero kuti awatumize mwina Kumwamba kapena ku gehena, kosaganizira kuti mwina analowetsedwa ndi Satana, kuphedwa ndi Manda, kapena anaotchedwa mpaka kufa.

Mulungu asanaikeko Buku la Moyo, mu limene maina a onse amene adzalowa mu Ufumu wosatha wa Kumwamba alembedwa. Kulinso Mabuku a Zochita, amene amalemba maina ndi machimo a onse amene adzaponyedwa mu gehena. Mu Mabukuwa a Zochita mmalembedwa machimo onse amene wina anachita pamene anali kukhala padzikoli lapansi. Zinthu zonsezi zimadalira pa Mulungu mchisomo Chake. Ambuye Ali Ndi Mitundu Iwiri ya Mabuku


Mulungu anagawa kale anthu chimodzimodzi mzigawo ziwiri malinga ndi mmene Iye anafunira. Chinapangidwa ndi Mulungu kuti akufa onse adzaukitsidwa, ndipo ndiyeno adzaima pamaso pa mabuku Ake awiri ndi kuweruzidwa. Mu Buku la Moyo mmalembedwa maina a okha amene anakhulupilira mwa Yesu pamene anali padzikoli lapansi, analandira chikhululukiro cha machimo awo, ndipo chonchi ndimmene kosalephera adzalowera mu Ufumu wa Kumwamba. Chiweruzo cha Mulungu chomaliza chidzaima pa mabuku awiri mmene dzina la wina linalembedwa. Mulungu anaika kale, mmawu ena, amene adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba ndipo nndi otani amene adzaponyedwa mgehena. 

Choncho Mulungu adzaukitsa akufa onse kukhalanso ndi moyo, adzatsegula Mabuku Ake, ndikuona mabuku awiri mu limene maina awo analembedwa. Ndipo ndiyeno Iye adzatumiza onse amene maina awo analembedwa mu Buku la Moyo Kumwamba, koma onse amene maina awo sadzapezeka mu Bukuli la Moyo, motsiyanitsa, mmalo mwake adzaponyedwa mgehena. Tiyenera kukuikako nzeru kudziwa ndi kukhulupilira mu zoonazi zokhazikitsidwa zopangidwa ndi Mulungu.

Kuti agamula amene ayenera kutumizidwa mgehena, Mulungu adzaukitsa akufa onse ndi kuwaweruza. Chinagamulidwa ndi Mulungu kuti Iye adzawaweruza malinga kuti mwina maina awo analembedwa mu Buku la Moyo kapena mu Buku la Zochita (Mabuku Achiweruzo). 

Kuli malo awiri Mulungu anakhazikitsa kale ya onse amene adzaima pamaso pa Iye. Adziwika kuti Kumwamba ndi gehena. Gehena ndi nyanja yamoto mmene lawi ndiponso sulufule uyaka. Mulungu anachigamula kuti onse amene maina awo sanalembedwe mu Buku la Moyo adzaponyedwa mnyanja yamoto, pamene onse amene maina awo analembedwa mu Bukuli la Moyo adzalandilidwa Kumwamba. 

Kumwamba, Mtengo wa Moya oima mmbali mwa mtsinje wa madzi a moyo, okhala ndi zipatso 12 malinga ndi nthawi yake. Kumwamba kokongolaku, oyera sadzakhala ndi matenda kapena kupweteka, koma adzakhala mosangalala kwa muyaya ndi Mulungu. tiyenera kukhulupilira mu choona chakuti Mulungu agamula kupereka Kumwambaku kwa Oyera. 

Onse amene sakhulupilira mwa Yesu, mnjira ina, maina awo analembedwa mu Buku la Zochita. Cifukwa zochita zonse zimene ochimwa anachita ndi zolembedwa mu Mabukuwa, Mulungu amatiuza kuti Iye adzawaponya mnyanja yamoto, kuti awalange cifukwa cha machimo awo olembedwa mu Bukuli, ndipo cifukwa cha uchimo wao osakhulupilira mwa Yesu. Cimene ndichofunikira kwambiri apa ndi mu Buku liti mmene maina anu ndi langa linalembedwa. 

Pamene tikhali kukhala padzikoli lapansi, tiynera vkudzindikira kuti umoyo wa padzikoli lapansi sikuti ndi onse ulipo. Monga mmene Masalimo 90:10 imatiuzira, “Masiku amoyo wathu amangokwana zaka 70, Ndipo ngati tili ndimphamvu yapadera amakwana zaka 80. Koma ngakhale zili choncho, amangodzaza ndi mavuto ndi zopweteka. Pakuti masiku amene timakhala ndi moyo amatha mwamsanga ndipo timachoka mofulumira.” Ngakhale kuti tinali kukhala padzikoli lapansi kwa zaka 70 kapena ngakhalenso 80, mwamsanga kapena posachedwa tonse tidzaima pamaso pa Mulungu. ndipo ngati taima chonchi pamaso pa Ambuye athu pomaliza, zonse zofunikira zili mu Buku limene maina athu analembedwa, mwina mu Buku la Moyo kapena mu Mabuku a zochita (Mabuku Achiweruzo), pakuti ichi chidzaima pa mwina dzife olandiridwa Kumwamba kapena tidzaponyedwa mnyanja yamoto. Tiyenera kubwera kukudzindikira kuti moyo padzikoli lapansi si ndi zinthu zonse.Iwo Amene Maina Awo Ndi Olembedwa mu Buku la Moyo


Tiyeni tiyaongane mu Luka 16:19-26: “Munthu wina wake anali wolemera, ndipo nthawi zonse anali kuvala zovala zofiirira zapamwamba ndi nsalu zabwino kwambiri. Iye anali kusangalala ndi kudyerera tsiku ndi tsiku. Koma munthu wina wopemphapempha dzina lake Lazaro, anali kumukhazika pachipata cha wachumayo, ali ndi zilonda thupi lonse. Iyeyo ankalakalaka kudya nyenyeswa zakugwa patebulo lawa chuma uja. Agalu nawonso anali kubwera kudzanyambita zilonda zakezo. Patapita nthawi wopemphapempha uja anamwalira ndipo angelo anamutenga kukamuika pachifuwa cha Abulahamu. “Munthu wachuma ujanso anamwalira ndipo anaikidwa m’manda. Ali m’Mandamo anakweza maso ake, ali mkati mozunzika, ndipo anaona Abulahamu kutali, ndipo Lazaro anali pachifuwa chake. Choncho anaitana kuti, ‘Atate Abulahamu, g ndichitireni chifundo.Mutume Lazaro kuti aviike nsonga ya chala chake m’madzi kuti aziziritse lilime langa,h chifukwa ndikuzunzika m’moto wolilimawu.’ Koma Abulahamu anati, ‘Mwanawe, kumbukira kuti unalandiriratu zabwino zako zonse pamene unalimoyo, ndipo Lazaro analandiriratu zinthu zoipa. Koma tsopano akusangalala kuno ndipo iwe ukuzunzika. Komanso, paikidwa phompho lalikulu kwambiri pakati pa ife ndi anthu inu, lmoti ofuna kuolokera kumeneko kuchokera kuno sangathe. Komanso anthu sangaoloke kuchokera kumeneko kubwera kuno.’” 

Ndi ndimeyi, Yesu amaphunzitsa kuti Kumwamba ndi gehena kulikodi. Monga mmene munthu wolemera mndimeyi, anthu ambiri mbiri sakhulupilira kukhalako kwa Kumwamba ndi gehena. Abrahamu ndi tate wa chikhulupiliro. Apa ngati ikuti wopemphapempha Lazaro anaikidwa pa chifuwa cha Abulahamu, chitanthauza kuti, monga mmene Abrahamu anakhulupilira mu Mawu a Mulungu, Lazaro nayenso anakhulupilira mwa Yesu ngati M’pulumutsi wake, analandira chikululukiro cha machimo ake, ndipo kuchoka pamenepo anapita Kumwamba. Kukhala mdzikoli lapansi, tiyenera kupenyetsetsapo ndiponso kuganizirapo za malo a Lazaro ndi munthu wolemera. 

Mulungu amatiuza kuti kwa wina aliyense mzdikoli lapansi, umoyo mdzikoli lapansi si kuti ndi zinthu zones mwina mulimonse. Ngakhale wina agwire ntchito mozipereka kotani mu unoyo wa mdzikoli lapansi, si kuti iye angakwanitse kukhala moyo kwa zaka 70─80 zokha pafupifupi, koma zimene zingasalire iye pomaliza ndi kugwira ntchito yakalavula gaga ndiponso chisoni chokha. 

Mkukhala kwa miyoyo yathu, choncho, tonse tiyenera kukonzekera za umoyo wathu wakutsogolo. Ndipo tiyenera kuperekanso chikhulupiliro chathu ku ana athu, kotero kuti, naonso, akwanilitse kupita ku malo okoma. Chidzakhala chochitisa chisoni kotani ngati munthu, atakhala padzikoli lapansi, pomaliza kudzaima pamaso pa Mulungu kuti aweruzidwe kokha ndi kuponyendwa mnyanja yamoto? 

Kulibe munthu amene angasinthise zimene Mulungu akonza, kuti onse amene maina awo analembedwa mu Buku la Zochita adzaponyedwa mnyanja yamoto. Ndiyeno kuli njira imodzi imene ife tingapewere kuponyedwa mnyanja yamotoyi, ndipo iyi ndikuonetsetsa kuti maina athu alembedwa mu Buku la Moyo. Kuti tithawe kuchoka mnyanja yamoto, kulibe njira ina iliyonse koma kuti maina athu alembedwe mu Buku la Moyo. 

Kodi, ndiyeno, n’motani mmene maina athu angalembedwere mu Bukuli la Moyo? Monga mmene Lazaro anaikidwira pa chifuwa cha Abulahamu, choncho tiyenera kulandira chikhululukiro cha machismo athu podziwa ndi kukhulupilira nchito za chilungamo cha Mulungu (Aroma 5:18) kupyolera mu Mawu Ake. Ndiyeno ndipokhapo tingalowe Kumwamba. Kuti maina athu alembedwe mu Buku la Moyo, tiyenera kukhulupilira mwa Yesu. Yesu ndi Mulungu Iyeyekha ndiponso Mesiya wathu. Mesiya chitanthauza kuti Wina wache amene amapulumutsa onse amene amagwa mu uchimo. Ndi Yesu yekha amene angatipulumutse, amene, cifukwa cha machismo athu, tonse mwina mwake ndife agamulidwa kuti tiweruzidwe ndi Mulungu ndiponso kuponyedwa mnyanja yamoto. 

Ndani padzikoli lapansi sangachite uchimo wina uliwonse pamaso pa Mulungu, ndipo ndani pakati pathu ndi oyera 100 peresenti mzochita? Kulibe wina aliyense! Tiyenera kudzindikira kuti cifukwa tonse ndife odzaza ndi zolakwa, si tingalephere koma kugwa mu uchimo, ndipo cifukwa cha machimo athuwa ndife ogamulidwa kuti tiponyedwe mnyanja yamoto. 

Koma Mulungu anatumiza Yesu padzikoli lapansi kuti adzatipulumutse, ndani amene sangalephere koma kuponyendwa mnyanja yamoto cifukwa cha machimo athu. Dzina loti “Yesu” litanthauza kuti ‘Wina amene adzapulumutsa anthu Ake kuchoka ku machimo awo’ (Mateyu 1:21). Choncho, tingalowe Kumwamba pokhapo ngati takhulupilira mchoonadi chakuti Yesu anabwera padzikoli lapansi ndi kutipulumutsa kuchoka ku machimo athu onse ndi ntchito Zake za chilungamo. Kodi Ndiyeno ndi Otani amene Adzaponyedwa M’nyanja Yamoto


Chivumbulutso 21:8 imatiuza amene adzaponyedwa m’nyanja yamoto: “Koma amantha, opanda chikhulupiriro, odetsedwa amenenso amachita zinthu zonyansa, opha anthu, adama, wochita zamizimu, opembedza mafano, ndi onse abodza, gawo lawo lidzakhala m’nyanja yoyaka moto ndi sulufule. Nyanja imeneyi ikuimira imfa yachiwiri.” 

Poyamba pa zonse, kodi ndani amene Baibulo limamuyerekeza ndi mawu akuti “amantha?” aimilira ozitcha Akristu amene analephera kulandira chikhululukiro cha machimo awo kupitila mu uthenga wa madzi ndi Mzimu, ndipo choncho ali ndi mantha pamaso pa Mulungu ngakhale kuti okhulupilira mwa Yesu mwina mwache. Mulunga anakonza kuti anthu otero adzaponyedwa m’nyanja yamoto. Mulungu akonzanso kuti onse amene ndi osakhulupilira, odetsedwaopha anthu, adama, ochita zamizimu, opembeza mafano, ndin onse abodza onse adzaponedwa mgehena. 

Mwa mwambo, munali opembeza mafano ambiri mu Koliya. Ngakhale tsopanoli, si chachilendo kuona akugwada pamaso pa zifaniziro za zolengedwa za Mulungu ndi kupereka mapemphero kwa izo. Anthu amachita tero cifukwa ndi mbuli ndiponso ndi opusa. Mulungu amadana nacho ngati anthu amapembeza zinthu zopanda moyo monga ndi za umulungu. 

Mulungu analenga munthu muchifaniziro Chake (Genesis 1:27). Munthu nayeso ndiye mbuye wa zolengedwa zonse. Ichi ndicho cifukwa tiyenera kukhulupilira mwa Mulungu. Cifukwa tili muchifaniziro Chake cha Mulungu, tamakhalapo kwa muyaya, monga mmene Mulungu Iyeyekha amakhalapo kwa muyaya. Kuli dziko losatha la ife pambuyo pa imfa yathu. Ichi ndicho cifukwa Mulungu anatiuza kuti tizimupembeza Iye, Mulungu Yekhayo wosatha. Kodi, ndiyeno, n’ciani chidzachitika ngati tagwada pamaso pa zolengedwa zachabechabe za Mulungu? tikanakhala ochita uchimo waukulu ochimwira Mulungu, cifukwa tikanakhala ochita chinthu cimene Mulungu amadana nacho kwambiri: kupembeza mafano. Anthu akanakhala opusa kwambiri ndiponso zitsiru kwambiri. Mulungu anagamula, tiyenera kudzindikira, kuti onse amene ali ndi mtunduu wa chikhulupiliro chosokonekera onse adzaponyedwa m’nyanja yamoto. 

Anthu amene adzaponyedwa mgehena adzafa kawiri. Ichi ndi cimene Mulungu Iyeyekha anagamula. Imfa yoyamba imabwera pothera pa miyoyo yawo yobvutidwa padzikoli lapansi, pambuyo poyendayenda mdzikoli lotopa. Kawiri kawiri chimanenedwa kuti wina amene okhala pa mendo anayi poyamba, ndiyeno pa mendo awiri, ndiyeno pomaliza pa mendo atatu, pothera kungofa kokha, ndi anthu iwo okha. 

Atafa kamodzi kokha mnjirayi, ngati anthu aima pamaso pa Mulungu ngati ochimwa, onse adzakumana ndi chiweruzo chao, ndipo ndi panthawiyi pamene imfa yachiwiri, wina amene sadzatha koma adzakhala kwa muyaya, adzawayendera iwo, mmaonekedwe oponyedwa m’nyanja yamoto. Iwo akanakhala kuti adzafera m’nyanjayi yamoto, iwo akanamasukako pang’ono kuchoka kumazunzo ake. Koma mmalowa ngakhale iwo afunitsitsa kuti afe, imfa idzathawa kuchoka kwa iwo.

Munthu aliyense alindifuniro lokhala kwa muyaya, kosakumana ndi imfa. Kukhalako kwa munthu, mchoona, ndi kosathadi, monga mmene anthu amafunira. Ichi ndicho cifukwa Baibulo, ngati wina afa, silimanena kuti wafa, koma kugona tulo. Choncho tonse tiyenera kuthawa kuchoka kuimfa yachiwiri imene idzatiponya m’nyanja yamoto. Tonse tiyenera kudzindikira mmene zilili kuti tichite kotero kuti maina athu alembedwe mu Buku la Moyo. Ndipo kuti maina athu alembedwe mu Buku la Moyo, tiyenera kukhulupilira mwa Yesu moyenera. 

Anthu kawirikawiri amaganiza ndi kunena kuti Yesu, Buddha, Confuncius ndiponso Mohammad onse ndi athu, icho chilichabe bwino kukhala ngati munthu wabwino. Ndicho cifukwa iwo sangamvetsetse cifukwa cimene timaikapo nzeru kuti iwo akhulupilire mwa Yesu yokha. Koma onsewa ndi maganizo olakwika. Inu ndi Ine, chimodzimodzi ndi zinthu zina zilizonse mdzikoli lapansi, ndi zachabechabe koma zolengedwa zopanda phindu ndiponso anthu pamaso pa Mulungu. Koma ngati tayangana pa kubadwa kwa Yesu ndi zimene anakwanilitsa pamene anali pdzikoli lapansi, tonse tingadzindikire kuti Iye si munthu monga mmene alili ambiri ndi Nzeru zinayi. Iye ndi Mulungu Iyeyekha amene, adzapulumutsa anthu, anabwera padzikoli lapansi mmaonekedwe a munthu, ananyamula uchimo wathu one kupitila mu ubatizo Wake, analandira chilango chonse cha machimo anthu onse mmalo mwathu, ndipo ndimene anatsirizira nchito Yake yoombola anthu kuchoka ku machimo ku uchimo. 

Kubadwa kwa Khristu kunali kosiyana ndi kubadwa kwa anthu wamba. Ana ababwadwa pokhala malo amodzi kwa mwamuna ndi mkazi. Umu ndimmene wina aliyense amabadwira mdzikoli lapansi. Koma Yesu anadwa kwa namwali amene sanadziwepo mwamuna. Kuti atipulumutse ife anthu, ndipo mkukwanilitsa Mawu aulosi amene ananeneredwa zaka 700 zapita kupyolera mu Mneneri Yesaya, Yesu, amene ndi Mulungu Iyeyekha, anabadwa mdzikoli lapansi mthupi la munthu, kupyolera muthupi la namwali (Yesaya 7:14). Ndipo pamene anali padzikoli lapansi si kuti Iye anaukitsa akufa ndi kuchilitsa odwala ndiponso olemara okha koma Iye anapanganso machimo onse adziko lapansi kuzimiririka. 

Mulungu, Ambuye a zolengedwa amene anapanga dziko lonse, anabwera padzikoli lapansi ndipo anakhala munthu Iyeyekha kwa kanthawi kochepa, zonsezi kuti apulumutse mitundu onse ya anthu kuchoka ku machimo ake. Cifukwa cimene tiyenera kukhulupilira mwa Yesu ndi, poyamba pa zonse, cifukwa Iye ndi Mulungu Iyeyekha. Chachiwiri, cifukwa Iye anachotsa machimo athu onse, kotero kuti maina athu alembedwa mu Buku la Moyo, ndi kutipanga kukhala ana a Mulungu opanda uchimo. Kamodzi kokha tinabadwa padzikoli lapansi, tonse tiyenera kufanso kamodzi kokha, ndipo pambuyo pa imfa yathu tonse tiyenera kuweruzidwa. 

Koma Yesu anabwera padzikoli lapansi, ananyamula machimo athu onse ndi ubatizo Wake analandira kuchokera kwa Yohane, anaweruzidwa pa Mtanda mmalo mwathu, ndipo kuchoka pamenepo analora onse aife amene okhulupilira mwa Iye kukhala ndi Iye kwa muyaya mu Ufumu wosatha wa Kumwamba. Kuti atipulumutse kuchoka ka chiweruzo cha uchimo, mmawu ena, Mulungu Iyeyekha anatisuka ku machimo athu onse. Ichi ndicho cifukwa tonse tiyenera kukhulupilira mwa Yesu, Amene akhala M’pulumutsi. 

Yesu si munthu wamba. Cifukwa Mulungu analonjeza mitundu yonse ya anthu kuti Iye adzaipulumutsa, ndipo cifukwa kuti akwanilitse lonjezoli Iye anabwera padzikoli lapansi kupitila mthupi la namwali, ndipo cifukwa Iye anapulumutsadi onse kuchoka ku machimo awo, tonse tiyenera kukhulupilira mwa Yesu, amene ndi Mulungu Iyeyekha. Ngati takhulupilira mwa Yesu moyenera, maina athu adzalembedwa mu Buku la Moyo. Mulungu anatiuza kuti ndipokhapo tabadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu ndi pamene munthu anauone ndi kulowa mu Ufumu wa Kumwamba. Tonse tiyenera kukhulupilira mwa Yesu. Yesu Amene Anakhala Njira ya Kumwamba


Tiyenera, ndiyeno, kudziwa mmene Yesu anapangira machimo athu kuzimiririka. Kubwera padzikoli lapansi, Yesu anabatizidwa ndi Yohane mu Mtsinje wa Yordani (Mateyu 3:13-17). Iye analandira ubatizo Wake kuchokera kwa Yohane kotero kuti Iye anyamule machimo onse a anthu (kuphatikizapo anu ndi anga). Kupitila mmanja a Yohane M’batizi, oimililako anthu onse, uchimo uliwonse wa anthu onse unaikidwa pa Yesu. Atanyamula chonchi machimo onse adziko lapansi pa Iyeyekha kupitila mwa Yohane, ndiyeno Yesu anakhetsa magazi pa Mtanda ndi kufa pamenepo. Ndiyeno Iye anauka kuchoka kwa akufa mu matsiku atatu. 

Ambuye athu analonjeza kuti aliyense amene okhulupilira mwa Iye adzalandira moyo osatha. Mulungu anagamula kuti aliyense amene okhulupilira mchoonadi chakuti Yesu ananyamula machimo ake onse pa Iyeyekha ndipo analandira chilango chonse cha machimowa pa Mtanda sadzaponyedwa m’nyanja yamoto, koma mmalo mwake dzina lake lidzalembedwa mu Buku la Moyo. 

Yesu akunenena kuti mu Yohane 14:6, “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa Ine.” Anthu ayenera kukhulupilira mwa Yesu amene akhala njira ya Kumwamba. Yesu ndi M’pulumutsi wathu. Yesu ndi Mulungu wathu. Yesu ndi amene ndiponso choonadi chenicheni mdzikoli. Ndipo Yesu ndi Ambuye wa umoyo. Kuti tionetsetse kuti maina athu alembedwa mu Buku la Moyo ndi kuti momwemo talandiridwa mu Ufumu wa Kumwamba, tonse tiyenera kukhulupira mwa Yesu. 

Cifukwa Yesu ananyamuladi machimo athu ya anthu onse pa Iyeyekha polandira ubatizo Wake kuchokera kwa Yohane M’batizi mu Mtsinje wa Yordani, tiyenera kukhulupilira mwa Iye, Amene wakhala M’pulumutsi wopepetsera. Ndipo n’cifukwa chakuti Yesu anakwanilitsa chipulumutso chathu popachikidwa ndi pokhetsa magazi pa Mtanda ngati chilango cha machimo athu kotero kuti inu ndi Ine tsopano tingalowe Kumwamba.

Yesu nagamula amene adzaponyedwa m’nyanja yamoto. Onse amene sakhulupilira ndi amene ndi amantha onse adzaponyedwa m’nyanja yamoto cifukwa kopanda chikhulupiro kwao, koma choncho ndi mmene chidzakhalanso ku ana awo ndi m’badwo ukubwera. Kuti tifika pa wina kukhala-bwino mu uzimu ndiponso kuthupi, wina aliyense ayeneradi ndi kukhulupiliratu mwa Yesu. Kodi Chikanakhala Motani kuti Yesu Sanalandire Ubatizo Wake?


Mulungu ndi Amene yekhayo amapereka madalitso Ake kapena matemberero ku munthu aliyense. Ichi ndicho cifukwa tiyenera kukhulupilira mwa Iye. Kodi mkudziwa cifukwa cimene miyoyo ya anthu ambiri ndi yachisoni, cifukwa n’ciani mitundu ya dzikoli lapansi ikugwa? Ndi cifukwa chakuti Mulungu ananena kuti Iye adzatemberera onse amene akudana ndi Iye ndiponso kupembeza mafano kwa mibadwo itatu, inayi ikubwera. Koma Iye ananenanso kuti Iye adzadalitsa kwa mibadwo chikwi ikubwera onse amene atumikira ndi kukonda Mulungu ndiponso kusunga malamulo Ake (Ekisodo 20:5-6).

Ichi si chitanthauza kuti ngati wina akhulupilira mwa Yesu mwina mwache, iye ayenera kudalitsika mofikapo. Wina ayenera kukhulupilira mwa Yesu ndi kudziwa kwenikweni za Iye. Ngati anthu okhulupilira, mmawu ena, kuti Yesu ndi Mulungu Iyeyekha amene anabwera padzikoli lapansi, kuti Iye anasuka machimo awo onse powatenga machimowa pa Iyeyeka mwa ubatizo Wake, ndipo kuti Iye wakhala M’pulumutsi wao oona popachikidwa mmalo mwao—ngati iwo okhulupira, mwachidule, kuti Yesu ndi Mulungu wao ndiponso M’pulumutsi wao—Mulungu anati Iye ndiyeno adzadalitsa onse amene okhupilira tero kwa mibadwo 1000 ikubwera. 

Koma panthawi imodzi, Mulungu anatilonjezanso kuti Iye adzatemberera kwa mibadwo itatu, inayi ikubwera onse amene sakhulupilira mwa Yesu. Ichi ndicho cifukwa wina aliyense, palibe kanthu mmene iye aonekera, ayenera kudziwa ndi kukhulupilira mchoonadi cha kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Onse amene ali ndi chikhulupiliro chotero adzakhululukidwa machimo awo onse, adzalandira moyo osatha, adzalowa Kumwamba, chimodzimodzinso adzalandira, pamene okhalabe padzikoli lapansi, madalitso onse amene Mulungu anapatsa Abulahamu kale. 

Tonse tiyenera kukhala mu Mawuwa amene Mulungu anakonzera ife, ndipo chikhulupiliro chathu chiyenera kukhala malinga ndi mmene Mawu analembedwera. Tiyenera kudzindikihra ndi kukhulupilira mchoona kuti onse amene sakhulupilira mwa Mulungu adzaponyedwa mnyanja yamoto, koma onse amene okhulupilira, mosiyanitsa, maina awo adzalembedwa mu Buku la Moyo ndipo adzalandiridwa Kumwamba kwa Tsopano ndiponso Dziko lapansi. Ndipo tiyeneranso kukhulupilira kuti ena aife amene okhulupilira adzakhalanso ndi moyo. Kuti tibadwe mwatsopano chimakhala chotheka pokhapo mwa uthenga wa madzi ndi Mzimu. 

Monga mmene wina aliyense sangakhala kopanda madzi, uthenga wa ndi, limodzi ndi uthenga wa magazi, ndi ofunikira kwambiri pa chipulumutso chathu. Pamene Yesu anabatizidwa, Iye ananyamula machimo athu pa Iyeyekha. Ndipo Iye analowetsedwa mmadzi ndiponso ndiyeno anachotsedwa kuchoka mmadzi. Ichi chitanthauza imfa Yake pa Mtanda ndi kuukitsidwa Kwake. Ambuye athu, mmawu ena, anaweruzidwa cifukwa cha machimo athu onse mmalo mwathu. Ndipo kuchotsedwa kwa Ambuye mmadzi chiimilira kuukitsidwa Kwake. Ichi chitanthauzanso chiukitso chathu, cha ena aife amene okhulupilira. 

Timakhulupilira mozama kuti Yesu ananyamula machimo athu ndi ubatizo Wake. Kuti Yesu sanalandire ubatizo, kodi nciani chikanachitika ku ife? Kukanakhala kulibe njira ya ife kuti tithawe kuchoka mnyanja yamoto. Monga n’pamene kukanakhala kulibe mvula kulibe wina aliyense mdzikoli, dziko lapansi likhalapo cifukwa cha mvula. Chimodzimodzi, umu ndi mmene kufunikira kwa ubatizo wa Yesu kulili ku ife. Ndiponso, imfa Yake pa Mtanda ndiyofunikira chimodzimodzi, cifukwa ichi chitanthauza kuti Iye anaweruzidwa cifukwa cha machimo mmalo athu. Ngati timafuna kupulumuka kuchoka kutemberero la Mulungu ndi chiweruzo, tiyenera kukhulupilira mwa Yesu mofikapo. Ndipo ngati tifuna kuyeretsedwa kuchoka ku machimo athu, tiyenera kukhulupilira kuti machimo athu onse anaikidwa pa Yesu pamene Iye anabatizidwa. 

Chikhulupilira cha Chikristu si mtundu wa chipembezo cimene chimapanga anthu kunjenjema ndi mantha. Aliyense ayenera kukhulupilira mwa Yesu. Obadwa-mwatsopano afunika kubwera mu M’pingo wa obadwa-mwatsopano ndi kumva Mawu kuti alimbitsidwe mchikhulupiliro. 

Anthu ena akunenena kuti wina afunika kukhulupilira mwa Yesu ndi kugwira nchito zabwino kuti apulumutsidwe ndiponso kuti alandire madalitso, koma chonsechi ndi kunena kosocheretsa kwa amaboza. Indedi, tiyenera kukhala ngati Akristu olungama ochita nchito zabwino, koma monga mmene bvuto lapachiyambi cha chipulumutso lilili, khalidwe lathu ndi loipa kotero kuti kulibe wina aliyense wa ife angakhalenso miyoyo yathu yathupi yoyera kofikapo pa 100 peresenti. Ichi ndicho cifukwa onse amene akunena kuti wina afunika kupulumutsidwa kupitila mu nchito zabwino ndi amaboza amene sakudziwa uthenga wa madzi ndi Mzimu ndiponso amene asocheretsa anthu. 

Ngati tadzindikira tokha kuti ndife ogamulidwa kuchita uchimo kuchokera pachiyambi, tikasinkhasinkha pa ubatizo wa Yesu Khristu umene analanndira ndiponso Mtanda umene ananyamula wa ife kuchokera mu Mawu olembedwa a Mulungu, ndiponso ngati tamvomera zonse zinthuzi, ndipokhapo tingakhale olungama, amene mitima yawo ndi yopanda uchimo, ndipo ofikapo kulowa Kumwamba. Mzimu Woyera usanakhale mwa ife ndi kutitsogolera, palibe wina aliyense wa ife angakhale wabwino, ngakhale tingayetse mwa mphamvu kotani. 

Mulungu anatipulumutsa popanga machismo athu kuzimiririka. Mmalo motiponya mnyanja yamoto oyaka kwa muyaya, Iye analemba maina athu mu Buku la Moyo, anatipatsa Kumwamba kwa Tsopano ndipo Dziko lapansi, ndiponso, monga mmene akwatibwi amazikongoletsa iwo okha kudikhira Mkwati, Iye nayenso, anatipatsa nyumba yochereza bwino ndiponso yokongola kwambiri, munda, ndi maluwa. Ndiponso Iye adzachotsa matenda onse kuchopka kwa ife, ndipo adzakhala ndi ife kwa muyaya mu Ufumu Wake. Tifunika kukhulupilira mwa Yesu cifukwa cha umoyo wathu wakutsogolo tikafa, koma tiyeneranso kukhulupilira mwa Iye cifukwa cha umoyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Cifukwa cha ana athu, nachonnso, tiyenera kukhulupilira. 

Kodi mfuna kulandilidwa Kumwamba, kapena mfuna kuponyedwa mnyanja yamoto? Kodi ndi mtundu wotani wacholowa cimene mdzasiira ana anu? Ngakhale kuti mumakumana ndi zobvuta ndiponso masautso a chikhulupiliro chanu mwa Yesu, muyenera kukhulupililabe mwa Iye, cifukwa kuchita tero kudzabweretsa madalitso aakulu pamose inu ndi ana anu. 

Okondedwa anga oyera, kupitila mu Mawu Ake, Mulungu anatiuza cifukwa cimene tiyenera kulalikira uthenga wa madzi ndi Mzimu, ndiponso cifukwa cimene mabanja athu ayeneranso kupulumutsidwa. Ndipereka mathokozo anga kwa Mulungu.