Sermons

[21-1] < Chivumbulutso 21:1-27 > Mzinda Oyera Umene Ukutsika Kuchokera Kumwamba< Chivumbulutso 21:1-27 >

“Tsopano ndinaona kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, pakuti kumwamba kwakale ndi dziko lapansi lakale zinali zitachoka, ndipo kulibenso nyanja. Ndinaonanso mzinda woyera, Yerusalemu Watsopano, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu, utakonzedwa ngati mkwatibwi wokongoletsedwera mwamuna wake. Kenako ndinamva mawu ofuula kuchokera kumpando wachifumu, akuti: “Taonani! Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu. Iye adzakhala pamodzi nawo, ndipo iwo adzakhala anthu ake. Zoonadi, Mulunguyo adzakhala nawo. Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.” Ndipo wokhala pampando wachifumun anati: “Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.” Ananenanso kuti: “Lemba, pakutimawu awa ndi odalirika ndi oona.” Anandiuzanso kuti: “Zakwaniritsidwa! Ine ndine Alefa ndi Omega, chiyambi ndi mapeto. Aliyensewomva ludzu, ndidzamupatsa madzi a m’kasupe wa moyo kwaulere. Aliyense wopambana pa nkhondo adzalandira zimenezi monga cholowa. Ineyo ndidzakhala Mulungu wake, r ndipo iye adzakhala mwana wanga. Koma amantha, opanda chikhulupiriro, odetsedwa amenenso amachita zinthu zonyansa, opha anthu, adama, ochita zamizimu, opembedza mafano, ndi onse abodza, gawo lawo lidzakhala m’nyanja yoyaka moto ndi sulufule. Nyanja imeneyi ikuimira imfa yachiwiri.” Ndipo kunabwera mmodzi wa angelo 7 aja, amene anali ndi mbale 7 zodzaza ndi miliria 7 yotsiriza. Iye anandiuza kuti: “Bwera kuno ndikuonetse mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa.” Choncho, mu mphamvu ya mzimu, ananditengera kuphiri lalikulu ndi lalitali, ndipo anandionetsa mzinda woyera, Yerusalemu, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu, uli ndi ulemerero wa Mulungu. Unali wonyezimira ngatimwala wamtengo wapatali kwambiri, ngati mwala wa yasipi wowala mbee! ngati galasi. Mzindawo unali ndi mpanda waukulu ndi wautali, ndipo unali ndi zipata 12. Pazipatazo panali angelo 12, ndipo panalembedwa mayina amafuko 12 a ana a Isiraeli. Kum’mawakwa mzindawo kunali zipata zitatu, kumpoto zipata zitatu, kum’mwera zipata zitatu, ndipo kumadzulo kwake zipata zitatu. Mpanda wa mzindawo unalinso ndi miyala yomangira maziko yokwana 12, ndipo pamiyalayo panali mayina 12 a atumwi 12 a Mwanawankhosa. Tsopano amene anali kundilankhula uja ananyamula bango lagolide loyezera, kuti ayeze mzindawo, zipata zake, ndi mpanda wake. Mzindawo unali ndi mbali zinayi zofanana kutalika kwake. M’litali mwake n’chimodzimodzi ndi m’lifupi mwake. Mngeloyo anayeza mzindawoo ndi bangolo, ndipo anapeza kuti unali masitadiya 12,000 kuuzungulira. M’litali mwake, m’lifupi mwake, ndi msinkhu wake, n’zofanana. Anayezanso mpanda wake, ndipo unali wautali mikono 144, malinga ndi muyezo wa munthu, umene ulinso wofanana ndi muyezo wa mngelo. Mpandawo unali womangidwa ndi mwala wa yasipi, a ndipo mzindawo unali womangidwa ndi golidewoyenga bwino woonekera ngati galasi. Maziko a mpanda wa mzindawo anawakongoletsa ndi miyala yamtengo wapatali ya mitundu yonse: maziko oyamba anali amwala wa yasipi, achiwiri wa safiro, achitatu wa kalikedo, achinayi wa emarodi, achisanu wa sadonu, a 6 wa sadiyo, a 7 wa kulusolito, a 8 wa belulo, a 9 wa topazi, a 10 wa kulusopurazo, a 11 wa huwakinto, ndipo a 12, wa ametusito. Komanso zitseko za pazipata 12 zija zinali ngale 12. Chitseko chilichonse chinali ngale imodzi. Ndipo msewu waukulu wa mumzindawo unali wopangidwa ndi golide woyenga bwino woonekera ngati galasi. Sindinaone kachisi mumzindawo, pakuti Yehova Mulungu Wamphamvuyonse ndiye anali kachisi wake, komanso Mwanawankhosa ndiye kachisi wake. Mzindawo sunafunikirenso kuwala kwa dzuwa kapena kwa mwezi, pakuti ulemerero wa Mulungu unauwalitsa, ndipo nyale yake inali Mwanawankhosa. Mitundu ya anthu idzayenda mwa kuwala kwake, ndipo mafumu a dziko lapansi adzabweretsa ulemerero wawo mumzindawo. Zipata zake sizidzatsekedwa n’komwe masana, ndipo usiku sudzakhalako. Iwo adzabweretsa ulemerero ndi ulemu wa mitundu ya anthu mumzindawo. Koma chilichonse chosapatulika, ndi aliyense wochita zonyansa ndiponso wabodza, sadzalowa mumzindawo. Amene adzalowemo ndi okhawo olembedwa mumpukutu wa moyo, umene ndi wa Mwanawankhosa.”Kusanthula


Ndime ya 1: Tsopano ndinaona kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, pakuti kumwamba kwa kale ndi dziko lapansi lakale zinali zitachoka, ndipo kulibenso nyanja. 

Mawuwa atanthauza kuti Ambuye Mulungu wathu adzapereka Kumwamba Kwake kwa Tsopano ndi Dziko lapansi monga mphatso Yake kwa Oyera amene anatengako mbali mu chiukitso choyamba. Kuchoka pamenepo, oyera sadzakhala kumwamba koyamba ndi dziko lapansi, koma kwa tsopano, kumwamba kwachiwiri ndiponso dziko lapansi, dalitsoli ndi mphatso ya Mulungu limene Iye adzapereka ku oyera Ake. Mulungu adzapereka dalitso lotero ku oyera okha amene anatengako mbali mchiukitso choyamba. 

Amene ayenera kusungalala ndi dalitsoli, mmawu ena, ndi oyera amene analandira chikhululukiro cha cha uchimo pokhulupilira mu uthenga oyera wa madzi ndi Mzimu opatsidwa ndi Khristu. Ambuye athu ndi Mkwati wa oyera. Kuchokera tsopanoli, zimene zikuyembekeza akwatibwi ndi kubvekedwa mchitetezo cha Mkwati, madalitso, ndiponso mphamvu ngati akwati a Mkwati Mwanawankhosa wao, ndi kukhala mu ulemerero mu Ufumu Wake olemelekezeka. 


Ndime ya 2: Ndinaonanso mzinda woyera, Yerusalemu Watsopano, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu, utakonzedwa ngati mkwatibwi wokongoletsedwera mwamuna wake. 

Mulungu anakonza mzinda oyera wa oyera. Mzindau ndi mzinda wa Yerusalemu wa Tsopano, Nyumba Yoyera ya Mulungu. Nyumbayi inakozedwera oyera a Mulungu okha. Ndipo ichi chinakonzedwa mwa Yesu Khristu cha oyera, ngakhalenso Ambuye Mulungu wathu asanalenge dziko lonse. Choncho oyera sangaleke koma kumuyamikabe Ambuye Mulungu cifukwa cha chisomo Chake cha mphatso ndi kupereka ulemelero onse kwa Iye ndi chikulupiliro chao. 

Ndime ya 3: Kenako ndinamva mawu ofuula kuchokera kumpando wachifumu, akuti: “Taonani! Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu. Iye adzakhala pamodzi nawo, ndipo iwo adzakhala anthu ake. Zoonadi, Mulunguyo adzakhala nawo.” 

Kuchokera tsopanoli, oyera adzakhala ndi Ambuye mu Kachisi wa Mulungu kwa muyaya, zonsezi ndi mwa chisomo cha Mulungu, mphatso imene oyera adzalandira cifukwa cha chikhulupiliro chao mu Mawu a chipulumutso a madzi ndi Mzimu. Onse amene anabvala dalitso lolowera mu Kachisi wa Ambuye ndipponso kukhala ndi Iye choncho adzapereka mayamiko kwa Ambuye Mulungu kwa muyaya. 


Ndime ya 4: “Kum’mawakwa mzindawo kunali zipata zitatu, kumpoto zipata zitatu, kum’mwera zipata zitatu, ndipo kumadzulo kwake zipata zitatu.”

Tsopano pakuti Mulungu akukhala ndi oyera, sipadzakhalanso misozi ya chisoni, kapena kulira cifukwa chakutaya okondedwa awo, kapena kulira mkupwetekeka. 

Kupwetekeka kwao kwa kumwamba koyamba ndi dziko lapansi kudzazimiririka kuchoka ku miyoyo ya oyera, ndipo cimene chidzayembekeza oyera ndi kukhala miyoyo yawo yodala ndiponso yolemekezeka ndi Ambuye Mulungu wao Kumwamba Kwake ndiponso Dziko lapansi. Ambuye Mulungu wathu, akakhala Mulungu wa oyera, adzapanga zinthu zonse ndiponso zamera zonse kukhala za tsopano, kotero kuti kusadzakhalenso misozi ya chisoni, kapena kulira, kapena imfa, kapena matenda, kapena kulira mofuula, kapena china chilichonse cymene chinawapweteka padziko lapansi loyamba. 


Ndime ya 5: Ndipo wokhala pampando wachifumu anati: “Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.” Ananenanso kuti: “Lemba, pakuti mawu awa ndi odalirika ndi oona.”

Ambuye tsopano adzapanga zinthu zonse kukhala za tsopano, ndipo adzalenga kumwamba kwa tsopano ndiponso dziko lapansi. kupanga zolengedwa Zake kumwamba koyamba ndi dziko lapansi loyamba kuzimiririka, Iye adzapanga kwa tsopano, kumwamba kwa chiwiri ndiponso dziko lapansi. cimene ndimeyi imatiuza sikuti Mulungu adzalisundutsa lakale, koma mmalo mwake adzalenga dziko la tsopano. Choncho Mulungu adzapanga Kumwamba kwa Tsopano ndiponso Dziko lapansi ndi kukhala ndi oyera. Oyera amene adzatengako mbali mchiukitso choyamba adzatengakonse mbali ya dalitso Lake. Ichi ndi chinthu cimene anthu sayenera ndi kuchilota mwa maganizo-opangidwa ndi munthu, koma ndi cimene Mulungu anakonzera oyera Ake. Choncho oyera ndi zinthu zonse zimapereka ulemerero onse, mathokoza, ulemu ndiponso mayamiko kwa Mulungu cifukwa cha ntchitoyi yaikulu. 


Ndime ya 6: Anandiuzanso kuti: “Zakwaniritsidwa! Ine ndine Alefa ndi Omega, chiyambi ndi mapeto. Aliyense womva ludzu, ndidzamupatsa madzi a m’kasupe wa moyo kwaulere.”

Ambuye Mulungu wathu anakonza ndipo anakwaniritsa zonse zinthuzi, kuchokera pachiyambi peni-peni mpaka pa mapeto. Zonse zinthuzi zimene Ambuye anachita, Iye anzachita pa Iyeyekha ndiponso cifukwa cha oyera Ake. Tsopano oyera amatchedwa ngati “Khristu,” ndiponso anakhala anthu a Mulungu. Onse amene anakhala oyera a Mulungu cifukwa chokhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu tsopano akudzindikira kuti ngakhale amapereka mathokozo ndiponso mayamiko kwa Mulungu kwa muyaya, komabe sangamuthokoze kofikapo pa chikondi ndi nchito za Ambuye Mulungu. 

“Aliyense womva ludzu, ndidzamupatsa madzi a m’kasupe wa moyo kwaulere.” Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi, Ambuye anapereka a kasupe a madzi a moyo ku oyera. Ichi ndi mphatso yaikulu pa zonse imene Mulungu anaika pa oyera Ake. Tsopano oyera ayenerera kukhala kwa muyaya Kumwamba kwa Tsopano ndiponso mu Dziko lapansi ndi kumwa kuchokera m’kasupe wa moyo, mmene sadzamvanso ludzu kwa muyaya. Oyera tsopano akhala, mmawu ena, ana a Mulungu amene adzakhala ndi moyo osatha, monga Ambuye Mulungu, ndi kukhala mu ulemerero Wake. Ndipereka mathokozo ndi ulemerero kwa Ambuye Mulungu wathu kachiwirinso potipatsa dalitsoli lalikulu. Haleluya! 


Ndime ya 7: “Aliyense wopambana pa nkhondo adzalandira zimenezi monga cholowa. Ineyo ndidzakhala Mulungu wake, ndipo iye adzakhala mwana wanga.”

“Aliyense wopambana pa nkhondo” apa aimilira amene anateteza chikhulupiliro chao chopatsidwa ndi Ambuye. Chikhulupiliro chimalowa oyera onse kupambana dziko lapansi ndi adani a Mulungu, kufooka kwathu, ndi kuzunzidwa ndi Wosusa Khristu. 

Ndipereka mathokozo ndi ulemerero kwa Ambuye Mulungu wathu pakutipatsa kupambana mu zonse. Oyera amene okhulupilira Ambuye Mulungu apambana Wosusa Khristu mokwanila mwa chikhulupiliro chao. Ku wina nndiponso ku aliyense wa oyera, Ambuye Mulungu wathu anapereka chikhulupilirochi ndi cimenechi iwo onse angapambane mu nkhondo yawo yomenyana ndi adani awo onse. 

Mulungu tsopano analola oyera, amene napambana dziko lapansi ndiponso Wosusa Khristu mwa chikhulupiliro chao, kuti alowe Kumwamba Kwake kwa Tsopano ndi Dziko lapansi. Ambuye Mulungu wathu anapereka chikhulupiliro chopambana ku oyera Ake kotero kuti iwo alowe mu Ufumu Wake. Pakuti Mulungu anatipatsa chikhulupiliro cimene chimapambana Wosusa Khristu, Mulungu tsopano akhala Mulungu wathu, ndipo ife takhala ana Ake. Ndipereka mathokozo ndi mayamiko kwa Ambuye Mulungu wathu pakutipatsa chikhulupilirochi chopambana adani athu onse.


Ndime ya 8: “Koma amantha, opanda chikhulupiriro, odetsedwa amenenso amachita zinthu zonyansa, opha anthu, adama, ochita zamizimu, opembedza mafano, ndi onse abodza, gawo lawo lidzakhala m’nyanja yoyaka moto ndi sulufule. Nyanja imeneyi ikuimira imfa yachiwiri.” 

Mmtima Wake, Ambuye Mulungu wathu ndi Mulungu wa choonadi ndiponso Mulungu wa chikondi. Ndani, ndiyeno, ndi anthuwa amantha pamaso pa Mulungu? Awa ndi amene anabadwa mu uchimo wapachiyambi ndipo amene sanayeretsedwe ku machimo awo onse ndi Mawu a uthenga wa madzi ndi Mzimu opatsidwa ndi Ambuye. Cifukwa mkhalidwe lawo amapembeza kwambiri oipa koposa Mulungu, poyereyera akhala atumiki a Satana. Ndi cifukwa chakuti iwo opembeza oipa pamaso pa Ambuye Mulungu, ndiponso akonda ndi kusata mdima kwambiri koposa kuwala, kotero kuti iwo sangakhale ndi mantha pamaso pa Ambuye Mulungu. 

Mulungu mmtima Wake ndi kuwala. Choncho ndi choona chokhazikitsidwa kuti anthuwa amene pa iwo okha ndi mdima wamene ayenera kuoopa Mulungu. monga mmene miyyoyo ya amene ndi a Satana ikukonda mdima, iwo ndi amantha pamaso pa Mulungu amene ndi kuwala Iyeyekha. Ichi ndicho cifukwa ayenera kupereka zonyasa ndiponso kufooka kwao pamaso pa Mulungu ndi kulandira chikhululukiro cha machimo awo kuchokera kwa Iye. 

Onse “osakhulupilira,” amene mitima yawo chikhalire siikhulupilira muchikondi cha Ambuye Mulungu wathu ndiponso mu uthenga Wake wa madzi ndi Mzimu, ndi adani Ake ndiponso ochimwa aakulu pamaso pa Mulungu. Miyoyo yawo ndi yodetsedwa, ndipo amasusana ndi Mulungu, chikondi ndiponso amachita tchimo lililonse, amasatira zowonetsero zachinyengo, amapembeza mtundu uliwonse wa mafano, ndiponnso amalankhula mtundu uliwonse wa maboza. Choncho, ndi chiweruzo cholungama cha Mulungu onse adzaponyedwa mnyanja yoyaka moto ndi sulufule. Ichi ndi chilango chawo cha imfa yachiwiri. 

Mulungu sanalole Kumwamba Kwake kwa Tsopano ndiponso Dziko lapansi ku anthuwa amene ndi amantha pamaso pa Iye, amene sakhulupilira mu uthenga wa Mawu Ake wa madzi ndi Mzimu, ndiponso amene, atasandulitsidwa akapolo a Satana, anadetsedwa. Mmalo mwake, Ambuye athu alowalora chilango chosantha, kuponya onse aiwo (kuphatikizapo, opha anthu, adama, ochita zamizimu, opembeza mafano, ndinso amaboza onse) mnyanja yamoto ndi sulufule. Gehena, limene Mulungu adzawapatsa, ndi imfa yawo yachiwiri. 


Ndime ya 9: Ndipo kunabwera mmodzi wa angelo 7 aja, amene anali ndi mbale 7 zodzaza ndi miliria 7 yotsiriza. Iye anandiuza kuti: “Bwera kuno ndikuonetse mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa.”

Mmodzi wa angelo amene anabweretsa mulili umodzi wa milili ya mbale zisanu ndi ziwiri anati kwa Yohane, “Bwera kuno, ndikuonetse mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa.” Apa, “mkazi wa Mwanawankhosa” aimilira onse amene akhala akwatibwi a Yesu Khristu pokhulupilira ndi mitima yawo mu uthenga wa madzi ndi Mzimu opatsidwa ndi Iye. 

Ndime ya 10-11: Choncho, mu mphamvu ya mzimu, ananditengera kuphiri lalikulu ndi lalitali, ndipo anandionetsa mzinda woyera, Yerusalemu, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu, uli ndi ulemerero wa Mulungu. Unali wonyezimira ngatimwala wamtengo wapatali kwambiri, ngati mwala wa yasipi wowala mbee! ngati galasi.

“Mzinda waukulu, Yerusalemu Woyera” Uimilira Mzinda Woyera umene oyera adzakhala ndi Mkwati wao. Mzindau umene Yohane anaona unalidi okongola ndiponso wabwino. Unali waukulu mkusanipa kwake, okongoletsedwa ndi miyala yonyezimira ya mtengo wapatali mkati ndi kunja, ooneka bwino ndiponso owala. Mngelo anamuonetsa Yohane kumene akwatibwi a Yesu Khristu adzakhala ndi Mkwati. Mzindau Woyera wa Yerusalemu otsika kuchokera kumwamba ndi mphatso ya Mulungu imene Iye anaika pa mkazi wa Mwanawankhosa. 

Mzinda wa Yerusalemu uwala mbee, ndipo kuwala kwake kuli ngati kwa mwala wamtengo wapatali, ngati mwala wa yasipi, mbee ngati galasi. Choncho, ku onse amene okhala mmenemo, ulemerero wa Mulungu uli ndi iwo kwa muyaya. Ufumu wa Mulungu ndi wa kuwalako, ndipo choncho ndi okhawo amene anatsukidwa kuchoka ku mdima wao onse, kufooka ndiponso ku machimo awo onse angalowe mu mzindawu. Chotero, tonse tiyenera kukhulupilira kuti ife tilowe mu Mzindau Woyera, tiyenera kuphunzira, kudziwa, ndiponso kukhulupilira mu Mawu oona a uthenga wa madzi ndi Mzimu umene Ambuye athu anatipatsa. 


Ndime ya 12: Mzindawo unali ndi mpanda waukulu ndi wautali, ndipo unali ndi zipata 12. Pazipatazo panali angelo 12, ndipo panalembedwa mayina amafuko 12 a ana a Isiraeli:

Zipata za Mzindawo zinatetezedwa ndi angelo 12, ndipo paizo panalembedwa maina a mafuko 12 a ana a Israeli. Mzinda unali ndi “mpanda waukulu ndi wautali,” kutiuza kuti njira yolowera mu Mzindawo ndi yobvuta kwambiri. Kupulumutsidwa kuchoka ku machimo athu onse pamaso pa Mulungu, mmawu ena, ndichosatheka mwa mphamvu za munthu kapena mwa katundu wa dziko wa zolengedwa za Mulungu. 

Kuti tiomboledwe kuchoka ku machimo athu onse ndi kulowa mu Mzinda Woyera wa Mulungu, ndi chofunikira kwambiri ku ife kuti tikhala n’chikhulupiliro chimodzimodzi ndi cha ophunzira a Yesu 12, chikhulupiliro cimene chikhulupilira mchoonadi cha uthenga wa madzi ndi Mzimu. Choncho, kulibe wina aliyense amene alibe chikhulupilirochi mu uthenga wa madzi ndi Mzimu angalowe mu Mzindawu Woyera. Ichi ndicho cifukwa angelo 12 osankhidwa ndi Ambuye anateteza zipata zake. 

Mawu onena, “maina olembedwa paizo,” kumbali ina, amatiuza kuti eni ake a Mzindawo anasankhidwa kale. Eni ake ndi Mulungu ndi anthu Ake, pakuti Mzinda ndi wa anthu a Mulungu amene tsopano akhala ana Ake. 


Ndime ya 13: Kum’mawa kwa mzindawo kunali zipata zitatu, kumpoto zipata zitatu, kum’mwera zipata zitatu, ndipo kumadzulo kwake zipata zitatu.

Monga mmene zipata zitatu zinaikidwa kum’mawa kwa Mzinda, kumpoto, kum’mwera, ndi kumadzulo kwake kunaikidwanso zipata zitatu. Ichi chimationetsa kuti ndi okhawo amene analandira chikhululukiro cha uchimo pokhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu ndi mitima yawo angalowe mu Mzindawo. 


Ndime ya 14: Mpanda wa mzindawo unalinso ndi miyala yomangira maziko yokwana 12, ndipo pamiyalayo panali mayina 12 a atumwi 12 a Mwanawankhosa. 

Miyala yaikulu igwiritsidwa nchito bwino ngati maziko a zomanga manga kapena zolimbitsa. Mawu akuti ‘mwala’ agwiritsidwa nchito mu Baibulo kuimilira chikhulupiliro mwa Ambuye Mulungu wathu. Ndimeyi imatiuza kuti tilowe mu Mzimda Woyera wa Ambuye Mulungu, tiyenera kukhala ndi chikhulupiliro cymene Iye anapereka ku anthu, chikhulupiliro cimene chimakhulupilira mchipulumutso Chake choyenera kuchoka ku machimo athu onse. Chikhulupiliro cha oyera ndi chamtengo wapatali koposa miyala ya mtengo wapatali ya Mzimda Woyera. Ndime apa imatiuza kuti mpanda wa Mzinda unamangidwa pa maziko 12, ndipo pa iwo panalembedwa maina a atumwi a Mwanawankhosa. Ichi chimatiuza kuti Mzinda wa Mulungu umaloledwa ku okhawo amene ali ndin chikhulupiliro chofanana ndi cimene atumwi a Yesu Khristu anali nacho. 


Ndime ya 15: Tsopano amene anali kundilankhula uja ananyamula bango lagolide loyezera, kuti ayeze mzindawo, zipata zake, ndi mpanda wake. 

Mawuwa atanthauza kuti wina alowe mu Mzinda omangidwa ndi Mulungu, ayenera kukhala ndi mtundu wa chikhulupiliro chothokozedwa ndi Iye, mtundu umene ungamubweretsere chikhululukiro cha uchimo. Apa ikunena kuti mngelo amene analikulankhuza Yohane anali ndi bango lagolide kuti ayeze Mzinda. Ichi chitanthauza tifunika kukhulupilira kuti Ambuye athu anatipatsa madalitso onsewa mkati mu uthenga wa madzi ndi Mzimu. Monga, “Chikhulupiriro ndicho chiyembekezo chotsimikizika cha zinthu zoyembekezeredwa (Aheberi 11:1),” nzoonadi Mulungu anatiptsa Mzinda Woyera ndiponso Dziko lapansi, zinthu zimene ndi dzazikulu kopotsa zimene tinali kuyembekeza. 

Ndime ya 16: Mzindawo unali ndi mbali zinayi zofanana kutalika kwake. M’litali mwake n’chimodzimodzi ndi m’lifupi mwake. Mngeloyo anayeza mzindawoo ndi bangolo, ndipo anapeza kuti unali masitadiya 12,000 kuuzungulira. M’litali mwake, m’lifupi mwake, ndi msinkhu wake, n’zofanana.

Mzinda unapangidwa ndi mbali zinayi zofanana, mlitali mwake, m’lifupi, ndiponso m’kutalika kwake chimodzimodzi. Ichi chimatiuza kuti tonse tifunika kukhala ndi chikhulupiliro chobadwa mwatsopano ngati anthu a Mulungu pokhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu. Kukhala chinthu cha choonadi, Ambuye athu sadzalora wina aliyense amene Sali ndi chikhulupilirochi cheni cheni mu uthenga wa madzi ndi Mzimu kuti alowe mu Ufumu wa Mulungu. 

Kuli anthu ambiri amene ali ndi maganizo otero osadziwika bwino akuti adzalowa mu Mzinda Woyera pokhala Akristu kokha, ngakhale kuti iwo akukhalabe ndi uchimo. Koma Ambuye athu anapereka chipulumutso kuchoka ku uchimo ndi Mzimu Woyera ndiponso Iye anasandutsa anthu Ake okha amene okhulupilira mchoonadi kuti Iye anawakhululukira machimo awo onse kupitila mu ubatizo Wake padzikoli lapansi ndi magazi Ake pa Mtanda. Ichi ndi chikhulupiliro cimene Ambuye athu amafuna kwa ife. 


Ndime ya 17: Anayezanso mpanda wake, ndipo unali wautali mikono 144, malinga ndi muyezo wa munthu, umene ulinso wofanana ndi muyezo wa mngelo. 

Tanthauzo la mu Baibulo la nambala 4 ndi kubvutika. Chikhulupiliro cimene Ambuye amafuna kuchokera kwa ife si chinthu cymene wina aliyense angakhale nacho, koma chikhulupilirochi angakhale nacho ndi okhawo amene amvomera Mawu a Mulungu, ngakhale kuti iwo sangamvetsetse mofikapo ndi maganizo awo. Ngati Mkristu, ndi chosatheka kulowa mu Mzinda Woyera pokhulumulira pa Mtanda wa Yesu okha, ndi kuti Ambuye ndi Mulungu ndiponso M’pulumutsi. Kodi mkudziwa cimene Ambuye anatanthauza mu Yohane 3:5 pamene anati, “Yesu anayankha kuti: Ndithudi ndikukuuza, Munthu sangathe kulowa mu ufumu wa Mulungu atapanda kubadwa mwa madzi ndi mzimu?” Kodi mkudziwa tanthauzo la Ambuye lobwera padzikoli lapansi, kubatizidwa ndi Yohane, kunyamula machimo adziko lapansi mpaka pa Mtanda, ndi kukhetsa magazi Ake pomwepo? Ngati mngayankhe funsoli, mngamvetsetse zimene Ndilankhula apa. 


Ndime ya 18: Mpandawo unali womangidwa ndi mwala wa yasipi, a ndipo mzindawo unali womangidwa ndi golidewoyenga bwino woonekera ngati galasi. 

Ndimeyi imatiuza kuti chikhulupiliro cimene cimatilora kuti tilowe mu Mzinda Woyera wa Mulungu ndi choyera ndipo chilibe kanthundi china chilichonse cha dziko lapansi. 


Ndime ya 19-20: Maziko a mpanda wa mzindawo anawakongoletsa ndi miyala yamtengo wapatali ya mitundu yonse: maziko oyamba anali amwala wa yasipi, achiwiri wa safiro, achitatu wa kalikedo, achinayi wa emarodi, achisanu wa sadonu, a 6 wa sadiyo, a 7 wa kulusolito, a 8 wa belulo, a 9 wa topazi, a 10 wa kulusopurazo, a 11 wa huwakinto, ndipo a 12, wa ametusito.

Maziko a mpanda a Mzinda anakongoletsedwa ndi mtundu uliwonse wa miyala ya mtengo wapatali. Mawuwa amatiuza kuti tingacherezedwa ndi mitundun yotsiyana tsiyana ya chikhulupiliro kuchokera mu Mawu a Ambuye athu. Ndipo miyalayi ya mtengo wapatali imationetsa mitundu ya madalitso amene Ambuye athu adzapereka ku oyera Ake. 


Ndime ya 21: Komanso zitseko za pazipata 12 zija zinali ngale 12. Chitseko chilichonse chinali ngale imodzi. Ndipo msewu waukulu wa mumzindawo unali wopangidwa ndi golide woyenga bwino woonekera ngati galasi. 

Ngale itanthauza ‘Choonadi’ cha mu Baibulo (Mateyu 13:46). Enieni ofuna-funa choonadi mokondwera adzataya zonse zimene alinazo kuti apeza Choonadi chimene chingamupatsa iye moyo otsatha. Ndimeyi imatiuza kuti oyera amene adzalowa mu Mzinda Woyera afunika kukhala ndi kupilira kwakukulu pamene okhalabe padzikoli lapansi, kuima njii osagwendezeka pakati-kati pa chikhulupiliro chao mchoonadi. Onse amene okhulupilira mu Mawu achoonadi olankhulidwa ndi Mulungu, mmawu ena, afunika kukhala ndi kupilira kwakukulu kuti ateteze chikhulupiliro chao. 


Ndime ya 22-23: Sindinaone kachisi mumzindawo, pakuti Yehova Mulungu Wamphamvuyonse ndiye anali kachisi wake, komanso Mwanawankhosa ndiye kachisi wake. 23 Mzindawo sunafunikirenso kuwala kwa dzuwa kapena kwa mwezi, pakuti ulemerero wa Mulungu unauwalitsa, ndipo nyale yake inali Mwanawankhosa.

Ndimeyi itanthauza kuti oyera onse adzalandiridwa mu manja a Yesu Khristu, Fumu ya mafumu. Ndipo Mzinda Woyera wa Yerusalemu siudzafunikiranso kuwala kwa dzuwa loyamba kapena mwezi, cifukwa Yesu Khristu, kuwala kwa dziko, adzakuchotsa. 


Ndime ya 24: “Mitundu ya anthu idzayenda mwa kuwala kwake, ndipo mafumu a dziko lapansi adzabweretsa ulemerero wawo mumzindawo.”

Ndimeyi imatiuza kuti anthu amene anakhalamo mu Ufumu wa zaka Chikwi chimodzi tsopano adzalowa Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi. “Mafumu a dziko lapansi” apa aimilira oyera amene anali kukhala mu Ufumu wa zaka Chikwi chimodzi. Mafumuwa adziko lapansi, ndime ipitiliza, “adzabweretsa ulemerero ndi ulemu mmzindawo.” Ichi chimatiuza kuti oyera amene anali atakhala kale mu mathupi awo aulemerero tsopano adzayenda kuchoka mu Ufumu wa zaka Chikwi chimodzi kupita ku Ufumu wa Mulungu olengedwa mwatsopano ndi Dziko lapansi. 

Choncho, ndi okhawo amene anabadwa mwatsopano pokhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu pamene anali kukhala mdziko lapansi ndipo chotero anakwatulidwa kuti akhale mu Ufumu wa Yesu Khristu kwa zaka chikwi chimodzi adzakwanitsa kulowa mu Mzinda Woyera wa Yerusalemu. 


Ndime ya 25: Zipata zake sizidzatsekedwa n’komwe masana, (usiku sudzakhalako). 

Pakuti Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi, kumene Mzinda Woyera unakhazikitsidwa, kunadzaza kale ndi kuwala koyera, sikungakhale usiku, ngakhale choipa china chilichonse. 


Ndime ya 26: Iwo adzabweretsa ulemerero ndi ulemu wa mitundu ya anthu mumzindawo.

Chi chimatiuza kuti kupitila mu mphamvu yodabwitsa ya Ambuye Mulungu, onse amene anali kukhala mu Ufumu wa Khristu kwa zaka chikhwi tsopano tsopano ndi oyenerera kupita mu Ufumu wa Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi, Ufumu umene Mzinda Woyera ukuimilira. 


Ndime ya 27: Koma chilichonse chosapatulika, ndi aliyense wochita zonyansa ndiponso wabodza, sadzalowa mumzindawo. Amene adzalowemo ndi okhawo olembedwa mumpukutu wa moyo, umene ndi wa Mwanawankhosa.

Pakati pa onse Akristu ndi amene sali-Akristu adzikoli lapansi limodzi, onse amene sakudziwa choonadi cha uthenga wa madzi ndi Mzimu ndi otsapatulika, onyansa, ndiponso amabodza. Iwo choncho sangalowe mu Mzinda Woyera. 

Mawu a Mulungu apa akutilora kuti titsimikize mmene kukula kwa mphamvu ya uthenga wa madzi ndi Mzimu imene Ambuye anatipatsa padzikoli lapansi kulili. Ngakhale kuti uthenga wa madzi ndi Mzimu walalikidwa ku anthu ambiri padzikoli lapansi, kunali nthawi zina pamene uthengawu unasulidwa ndi kukanidwa ngakhalenso ndi otchedwa-Akristu. Koma chikhulupiliro chokha mu uthenga wa madzi ndi Mzimu opatsidwa ndi Ambuye ndiwo kiyi wa Kumwamba. 

Anthu ambiri okhalabe osadziwa choonadichi, koma muyenera kudziwa kuti wina aliyense amene akudzindikira ndi kukhulupilira kuti uthenga wa madzi ndi Mzimu umene Ambuye anamupatsa iye ndi kiyi wa Kumwamba ndiponos wa kuchikhululukiro cha uchimo, dzina lake lidzalembedwa mu Buku la Moyo. 

Ngati mkumvomereza ndi kukhulupilira mu choonadi cha uthenga wa madzi ndi Mzimu, mdzabvekedwa ndi dalitso lolowera mu Mzinda Woyera.