Sermons

[21-2] < Chivumbulutso 21:1-27 > Tiyenera Kukhala ndi Mtundu wa Chikhulupiliro Cimene N’chotokozedwa ndi Mulungu< Chivumbulutso 21:1-27 >


Mulunga anatipatsa Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi. Mulungu akutiuza kuti zimene mkuona tsopano, kumwamba koyamba ndi dziko lapansi, ndi zonse zimene zili mmenemo, zidzazimiririka, ndi kuti Iye adzatipatsa mmalo a zimenezo kumwamba kwa tsopano, dziko lapansi la tsopano, ndi nyanja ya tsopano, ndiponso kubwezerapo zonse zinthu mu dziko lolengedwa mwatsopano. Ichi chitanthauza kut Ambuye Muloungu adzapereka Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi kukhala mphatso Yake ku oyera amene anatengako mbali mchiukitso choyamba. Dalitsoli ndi mphatso kuchokera kwa Mulungu imene Iye adzaika pa oyera Ake, amene analandira chikhululukiro cha uchimo wao. 

Choncho Mulungu adzapereka dalitsoli ku oyera amene anatengako mbali muchiukitso choyamba. Dalitspoli ndi lololedwa ku oyera okha amene, pokhulupilira mu uthenga woyera wa madzi ndi Mzimu opatsidwa ndi Yesu Khristu, analandira chikhululukiro cha machimo awo. Ambuye anthu choncho n’mmene adzakhalila Mkwati wa oyera. Kuchokera tsopanoli, chimene chasala ku akwatibwi kuchita ndi kubvala chitetezo cha Mkwati, madalitso, ndi mphamvu ngati akazi a Mwanawankhosa, ndi kukhala mu ulemerero mu Ufumu Wake olemekezeka kwa muyaya. 

Ndime imatiuzanso kuti Mzinda Woyera, Yerusalemu wa Tsopano unali okongola ngati mkwatibwi okongoletsedwa mfumu wake, kutsika kuchokera Kumwamba.

Mulungu anakonza mzinda woyera wa oyera. Mzindawo ndi mzinda wa Yerusalemu, Kachisi wa Mulungu. Kachisiyu ndi okonzedwera oyera a Mulungu okha. Ndipo unakonzedwera oyera onse limodzi mwa Yesu Khristu, ngakhale Mulungu asanalenge dziko. Oyera choncho sangaleke koma kumayamika Ambuye Mulungu ndi chikhulupiliro chao ndi kupereka ulemereo ku Iye cifukwa cha mphatsoyi ya chisomo. 

Zinthu zonsezi—kuti oyera asandulitsidwa anthu a Mulungu ndi kuti Iye n’mmene akhala Mulungu wao—ndi chisomo choikidwa ndi Mulungu ndiponso ndi mphatso imene oyera analandira kuchokera kwa Iye cifukwa chokhulupilira mu Mawu a chipulumutso a madzi ndi Mzimu. 

Choncho, onse amene ndi odalitsika kulowa mu Kachisi ka Ambuye ndi kukhala ndi Iye adzapereka mathokoza ndiponso ulemerero kwa Mulungu kwa muyaya, pakuti Malemba akutiuza kuti Mulungu adzachotsa misozi yawo, kotero kuti sikudzakhalanso imfa, kapena kulira, kapena kubvutika, ndi kuti zinthu zakale zidzatha. Ngakhale chisoni, kulira, kupweteka, imfa, kulira kofuula, ndiponso kugwetsa nkhope kulikobe tsopano mdziko lapansi, Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi, zinthu zonse zotero zidzatha. Onse amene adzakhala Kumwamba kwa Tsopano ndi dziko lapansi lopatsidwa ndi Ambuye sadzakhetsanso misozi iliyonse ya chisoni kapena kulira cifukwa cha chifundo cha kutaya kwa okondedwa awo, ainso. 

Ngati nthawi yolowera Kumwamba kwa Tsopano ya oyera yabwera, kumwamba koyamba, dziko lapansi loyamba, ndi chisoni chake chonse mwazizizi kudzazimiririka, ndipo cimene chidzayembekeza oyera ndi kukhala miyoyo yawo ya ulemerero ndiponso ya madalitso onse ndi Mulungu Kumwambaku kwa Tsopano ndi Dziko lapansi kwa muyaya. Mulungu adzachotsa maonekedwe oipa adziko loyamba ndi kupanga dzikoli la tsopano mwa ungwiro. 

Ndime tawerenga ya chapitala 21 imatiuza za Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi, limene lidzasatira pambuyo pa chionongeko cha dzikoli, utapita Ufumu wa zaka chikwi omasulidwa mu chapitala 20 chapita. Ndi chapitala 20, chilichonse cymene ndi chigwirizana ndi dzikoli lapansi chidzatha. Nthawi ya Wosusa Khristu (chilombo), alosi achinyengo, omusatira ake, ndiponso za amene sanakhulupilire mwa Mulungu koma akhala ali kususana ndi Iye mdzikoli, onse adzatha. Monga mmene iwo onse adzaponyedwa mu moto ngati Ufumu wa zaka chikwi watsekedwa, tsopano malo okha amene angaonekeremo ndi mgehena. 

Choncho, mu chapitala 21, Mulungu amatiuza za Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi kuti Iye adzapereka ku oyera, malo aungwiro kumene uchimwa sangapezekenso. Monga mmene ngati mfuna kuona nyama za mnkhalango mmapita ku zoo, ngati nthawiyi yabwera, wina aliyense amene afuna kuona Satana ndiponso omusatira ake adzafunika kupanga ulendo wa ku gehena. 

Mmalo amene Mulungu adzapatsa ife Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi, Ambuye athu, naonso, adzakhala ndi ife. Mulungu anatipangilanso Mzinda Woyera ndi maonekedwe okongola ndiponso munda wamusipu owala. Ngati Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi kubwera, zinthu zonse za dziko loyamba ndi maonekedwe ake oipa kudzazimiririka, choonadi chokha chidzakhalabe, ndipo oyera angwiro adzalamulira Ufumu wonse wa Kumwamba kwa muyayaya. Msade Nkhawa ndi Maonekedwe Anu Atsopanoli


Nthawiyi ya tsopano ndi nthawi ya mdima ndiponso yopanda chiyembekezo. Chiyembekezo sichipezeka kulikonse mnthawiyi, imene tsogolo lake ndilophimbidwa ndi chikaiko. Ichi ndicho cifukwa, pa nthawi zina, timamva kubvutidwa ndipo kufooka ngakhale pamene tili kulalika uthenga. Monga pa ine nekha, mtima wane kawiri kawiri wakhala ododoma cifukwa cha ichi, koma pamene ndili kuwerenga Mawu a Chivumbulutso ndi kumasulira ndime zake, Ndidzindikira kuti oyera ndi atumiki a Mulungu akakumana ndi nthawi zomaliza alibe chowadetsa nkhawa. Pondipanga kuti ndidzindikire kuti masautso ndi mazunzo a tsopanoli ndi a nthawi yochepa chabe, ndi kuti dziko lokongola likuima pamaso panga, Mulungu analimbitsa mtima wanga kotero kuti ndisabvutidwenso. 

Ngati tayangana maonekedwe athu okha a tsopanoli, chisoni ndi kusakhala ndi chidwi, miyoyo yathu ndi yodadi nkhawa ndi mazunzo osalekedza amene amationa pamene tilikutumikira uthenga. Koma cifukwa cha madalitso onse amene amatifika, ngakhale kuti sangaoneke ndi maso athu a thupi, mitima yathu ndiyomasuka ku kusacherezedwa konse, ndipo mmalo mwake ndi yodzaza ndi chiyembekezo chachikulu ndiponso chisangalalo. Cifukwa cimene palibilethu chifuniro cha ife kuti tikhale mu chisoni ndi cifukwa chakuti Mulungu anatipatsa kale Kumwamba Kwake kwa Tsopano ndi Dziko lapansi. 

Kodi mkhulupilira Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi? Ngakhale kuti mulibe kukuonapo, kodi munaganizapo za kumeneko?

Dziko lapansi, nalonso, lili ndi malo okongola. Ngati timalankhula za chilengedwe chokhala bwino mdzikoli lapansi, kawiri kawiri tikulankhula pa za mitengo, msipu okongola mu mbali mwa mitsinje, maluwa mu minda, ndi anthu abwino. Kuyeneranso kukhala madzi otsefukira obiliwira, ndiponso siliyenera kukhala ndi athu oipa, kapena kusowekera kanthu kena kalikonse. Ngati zonsezi zakwanilitsidwa, tikunena kuti ndi maonekedwe abwino kwambiri. Koma Kumwamba, zonse ndi zofikapo, kwambiri ndiponso kwa bwino koposa malo ena aliwonse mdziko lonse lingazitukumule ndi iwo. 

Funsoli ndi, ndiyeno, ndaini amene Mulungu anakonzera ndi kutsitsa kuchokera Kumwamba Mzindawo Woyera omangidwa mkongola. Mulungu anapanga Mzindawo kukhala wa oyera. Ichi ndichon cifukwa tonse tingaiware zinthu zonse za dziko loyamba. Ngakhale kuti tidzakhala mu ulemerero mu Ufumu wa zaka Chikwi, mdziko likubwera, Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi lomasulidwa mu chapitala 21, limene Mulungu moona afuna kutipatsa, tidzakhala ndi Ambuye ngakhalenso mu ulemerero waukulu. Kuti achite tero, Mulungu anatipulumutsa potitumizira Yesu Khristu, ndipo adzaukitsa ndi kutikwatura. Kukhala ndi Ambuye ndi mathupi angwiro ngati thupi la Yesu oukitsidwa kumaonetsa chifaniziro chithunzi-chooneka bwino cha moyo wokoma ndiponso odala umene umatiyembekeza. 

Kuti atipatse Ufumu wa Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi, Mulungu anapanga inu ndi ine kubadwa padzikoli lapansi, ndi Iye anatipulumutsa ife. Ngati oyera asiya dzikoli lapansi mwa chidzindikiro cha kuganizira pa chisomo cha Mulungu, onse angakhale bwino, kopanda kukumana ndi chobvuta chilichonse, kudzunzika ndi chisoni, kapena kukumana ndi nkhawa. Poyangana pa zimene Mulungu anachita ndi cymene Iye adzatichira kutsogola, tonse tingakhale okondwera ndiponso ofikapo. 

Koma ngati tayangana pa ife tokha ndiponso pa maonekedwe a zandale, zachitukuko, ndiposo pa makhalidwe a dziko lapansi opanda chiyembekezo, kulibe kusankha kwina kulikonse koma kugwera muchionongeko. Inu ndi Ine tisaiwale kuti Mulungu anatipatsa Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi, ndi kuti Kumwamba ndi kwathu. Ichi ndi choonadi. Ichi ndi choona. Ngakhale kuti dzikoli lapansi liyetsa-yetsa kukupangani kukhala muchisoni, msade nkhawa ndi ilo, kapena kukwiya, koma penyani kwa Ambuye. Ndipo khalani moyo wanu ndi chiyembekezo, kukhulupilira kuti Ambuye anaperekadi Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi ku oyera Ake. 

Mulungu anati Iye adzapanga zinthu zonse kukhala za tsopano. Iye anauza Yohane kuti alembe Mawuwa, kuti Iye adzapanga zinthu zonse kukhala za tsopano, “pakuti mawuwa ndi oona ndiponso okhulupirika.” Onse amene akutengako mbali muchiukitso choyamba adzatenganso mbali mu madalitso okhala mmalo amene Mulungu adzapanga zinthu zonse kukhgala za tsopano. Ichi ndi chinthu cimene sitingachiganizilepo ndi maganizo opangidwa ndi munthu, koma ndi chinthu china cimene Mulungu anakonzera oyera Ake. Oyera ndi zinthu zonse choncho adzapereka ulemerero, mathokozo, ulemu ndi mayamiko kwa Mulungu cifukwa chokwanilitsa nchitoyi yaikulu. 

Baibulo likuti, “Chikhulupiriroe ndicho chiyembekezo chotsimikizika cha zinthu zoyembekezeredwa, umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka (Aheberi 11.1).” Ngakhale kuti sitingazione zinthuzi ndi maso athu, mmawu ena, zonse n’zinthuzi n’zoona. Tinali ndi chiyembekezo kuti tipulumutsidwe kuchoka ku machimo athu onse, ndipo pokhulupilira muchipulumutso chathu tapulumutsidwadi. Ndipo cifukwa, titapulumutsidwa, tafuna ndi kuyembekezera kuti tikhala kwa muyaya mdziko lokwanira ndiponso labwino limene silisowekera kanthu kalikonse, Mulungu anakwalitsadi chiyembekezochi cha ife. Chinthu chilichonse cimene tinafuna ndi kuchiyembekezera zonse zidzaonekeradi, pakuti chiyembekezo chathu chonse ndi choona. 

Mu chapitala 10 cha Chivumbulutso, pamene Ambuye analankhuzana ndi Yohane kupitila mwa mngelo Wake amene anaima mwendo umodzi mnyanja wina pamtunda, ndipo pamene Yohane anafuna kuwalemba, Mulungu anamuuza kuti asalembe. Pakati pa zinthu zimene Ambuye analankhula, pali zinthu zina zimene Mulungu sanalore kuti zilembedwe, pakuti izi zinali zinsinsi zimene Iye anali kufuna kuzivumbulutsa ku ife oyera Ake okha.

Chinsinsichi ndi kukwatulidwa kwathu. Kudziwa penipeni pamene kukwatulidwa kwathu kudzachitikira, tiyenera kudzindikira kuti lipenga la 7 la Mulungu chidzindikiro chosocheretsa pakuthetsa chinsinsichi. Kodi, ndiyeno, n’liti pamene lipenga la 7 lidzalira? Lipenga la 7 lidzalira pamene zaka zitatu ndi hafu za nthawi ya zaka-7 ya Chisautso Chachikulu zapitako pang’ono. Apa ndi pamene chiukitso cha oyera ndi kukwatulidwa kudzachitikira. Ndipo ngati kukwatulidwa kwapita, milili yam bale 7 posachedwa idzasatilapo. 

Zaka dzapita kumbuyoku, Ndinali ndi msonkhano wa chitsitsimutso ndi mutu wake “Mipingo 7 ya mu Asiya Minor.” Ndinalembatso buku la mipingo 7 ya mu Asiya Minor, ndipo zamukati mwake zilingana ndi zimene ndamusulira mu ndime ya tsopanoyi apa. Kuyangana pa ziphunzitso mu buku, Ndingamve kuti, ngakhale nthawi zasintha mwadzizizi kwambiri, Mawu a Mulungu sanasinthe n’pang’ono pomwe kosayangana pakutha kwa nthawi. 

Kodi mfuna kukhala Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi, ku malo amene Mulungu anakonzera inu ndi ine? Maonekedwe oipa adzikoli sapezekakonso kumeneko. Pamene Mulungu ananena kuti Iye adzapanga zinthu zonse kukhala za tsopano, anthu ena anamasulira ichi ngati n’kunena kuti Iye adzasintha zimene zinalipo kale, monga ndi kubwezerapo. Koma kuchokera mu chapitala 21 ndi kupita kutsogola, ndi dziko la tsopano lonse, losiyaniranatu ndi la kale. Obadwa-mwatsopano adzatengako mbali za Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi lopangidwiratu la tsopano ndi Mulungu, pakuti ndi amene anatengako mbali mu mphamvu ya mmuzimu. Ndi, mmawu ena, pakuti iwo akhala otengako mbali mu ulamuliro wa muuzimu. 

Mmalo moika maganizo athu onse pa katundu, tiyenera kuganiza pa ndondomeka ya mmuuzimu. Ndipemphera kuti inu nonse mkhale mtundu wa oyera ndi atumiki amene okhulupilira mu zimene Mulungu anapereka ku miyoyo yathu, ndipo amene okhulupilira, muchikhulupiliro, kuti zinthuzi, ngakhale kuti zikhalibe kukwanilitsidwa, zidzakhalakodi. Mulungu anatipatsa madalitso aakulu. 

Mulungu anati Iye adzapereka kasupe wa madzi a moyo mwaulele ku onse okhala ndi ludzu. Mawuwa saimilira uthenga wa madzi ndi Mzimu. Ngati athu akhulupilira kuti Mulungu anawapulumutsa kuchoka ku ludzu lawo powapatsa uthenga Wake pa dzikoli lapansi ndi kuwapulumutsa kuchoka ku machimo awo, ichi, nachonso, n’chimodzimodzi ndikumwa madzi a moyo, koma ndime apa siimilira pa ichi chabe, koma aimilira madzi enieni amene adzamwedwa Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi, pamene wina aliyense amene adzamwa madziwa sadzafa, thupi lake lidzasanduka ngati lija la Ambuye, ndipo iye adzakhala kwa muyaya ndi Iye.

Ambuye athu anakonza ndi kukwanilitsa zonse zinthuzi, kuchokera pachiyambi peni peni mpaka ku mapeto. Zinthu zonse zimene Ambuye anachita, Iye anazichita pa Iyeyekha ndiponso za oyera Ake. Choncho, oyera tsopano atchedwa ngati Mulungu Iyeyekha ngati Khristu, ndipo akhala ana a Mulungu oona malinga ndi chikonzero Chake. Onse amene anakhala oyera pokhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu tsopano angadzindikire, kuchokera muchikhulupiliro chao mchikondichi chachikulu cha Mulungu ndi mu ntchito Zake zodabwitsa, kuti kulibe chosowekera cha iwo kuti kwa muyaya apereke mathokozo ndi mayamiko ku Ambuye. 

Monga mmene Ambuye anati, “Ndidzapereka akasupe a madzi a moyo ku iye amene wamva ludzu,” Iye anaperekadi akasupe wa madzi a moyo ku oyera Ake ndipo anawalora kusangalala moyo osatha. Iyi ndi mphoto yaikulu imene Mulungu anaika pa oyera Ake. Tsopano oyera adzakhala kwa muyaya Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi ndi kumwa kuchokera mu akasupe a madzi a moyo, kuchokera amene iwo sadzamvanso ludzu kwa muyaya. Oyera tsopano akhala, mmawu ena, ana a Mulungu amene adzakhala ndi moyo kwa muyaya, ngati Ambuye Mulungu, ndipo adzakhala mu ulemerero, Ndiperekanso mathokozo ndi ulemerero kwa Ambuye Mulungu cifukwa chotipatsa dalitsoli lalikulu.Chikhulupiliro mu Uthenga Oona Chipatipanga kuti Tipambane Dziko Lapansi.


Mtumwi Yohane tsopano abwereranso ku nthawi yake yatsopano. Ndime ya 7 akuti, “Aliyense wopambana pa nkhondo adzalandira zimenezi monga cholowa. Ineyo ndidzakhala Mulungu wake, ndipo iye adzakhala mwana Wanga.” “Iye wopambana” apa aimilira amene akuteteze chikhulupiliro chawo chopatsidwa ndi Ambuye. Chikhulupilirochi chikulora oyera onse kuti apambane mazunzo ndi mayetsero onse. Chikhulupiliro chathu mwa Ambuye Mulungu ndiponso mu chikondi choona mu uthenga wa madzi ndi Mzimu wopatsidwa ndi Iye ndi umene umatipatsa kupambana machimo onse adziko lapansi, chiweruzo cha Mulungu, adani athu, kufooka kwathu, ndi mazunzo a Wosusa Khristu. 

Ndipereka mathokozo ndi ulemerero kwa Ambuye Mulungu pakutipatsa kupambana pa zonse. Oyera amene okhulupilira mwa Ambuye Mulungu angapamabane Wosusa Khristu mwa chikhulupiliro chao, pakuti ku wina aliyense wa iwo, Ambuye Mulungu wathu anapereka chikhulupilirochi mu cimene iwo angagonjetsa adani awo onse mnkhondo yawo. Mulungu tsopano analora oyera, amene anapambana chonchi dziko lapansi ndi Wosusa Khristu mwa chikhulupiliro chao, kuti alowe Kumwamba Kwake kwa Tsopano ndi Dziko lapansi. ndipereka mathokozo ndi mayamiko kwa Ambuye Mulungu wathu potipatsa chikhulupilirochi cholimba. 

Mulungu ku onse amene akupamabna anati, Iye adzapereka Kumwamba Kwake kwa Tsopano ndi Dziko lapansi kukhala cholowa chao, kumene kulibe misozi, kapena chisoni, kapena nkhawa. Ndi okhawo amene akupambana amene ayenerera kukulandira. Chikhupululiro cha kupambanaku ndi chikhulupiliro mu uthenga wa madzi ndi Mzimu umene Ambuye anatipatsa. Ichi ndi chikhulupiliro mwa cimene tingapambane dziko lapannsi, machimo athu, kufooka kwathu, ndiponso Wosusa Khristu. 

Ngati mphatso ya chikhulupiliro chathu cimene chikupambana Wosusa Khristu, posatchedwapa tidzalandira Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi kuchokera kwa Mulungu. Pakuti tidzalandira madalitso onsewa a chikhulupiliro chathu, pamene Wosusa Khristu adzasusana nafe ndi kufuna kuchotsa chikhulupiliro chathu, tingagonjetsa chikonzero chonse cha adani athu onse mwa chikhulupiliro. Onse amene akupambana kukhulupilira mu Mawu a Mulungu palibe kanthu ngakhale zimene ena akulankhula kwa iwo, ndi kuteteza chikhulupiliro chao mchoonadi chakuti Ambuye anachotsa machimo awo onse. Onse aife amene, atalandira chikhululukiro cha machimo athu ndipo atabadwa mwatsopano, tsopano akukhala mnthawi za mapeto, ayenera kupambana zikonzero za Wosusa Khristu mwa chikhulupiliro chaso.

Tingagonjetse masautso okutha kwa nthawi-yochepa mwa chikhulupiliro chathu mchoonadi chakuti Ambuye anatipatsa Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi, limodzi ndi chuma chonse, ulemu ndi ulemerero. Pamene dziko labwino likutiyembekeza, kodi ife mchoonadi tipandukire uthenga wa chikhulupilirochi? Pamene mawa zinthu zabwino zikubwera kwa ife, pamene mwadzidzi zinthu zabwino zikutiyembekeza ngati tingapilire mu tsiku limodzi lokha, kodi sitingakwanitsa kupilira mu zobvuta za matsiku ano? Tonse tingapilire. 

Baibulo kawiri kawiri amatiuza za ‘chikhulupiliro, chiyembekezo ndi chikondi’ monga zinthu zofunikira zimene oyera afunika kusunga mmitima yawo. Onse amene ali n’chiyembekezo ndi opitilira pakugonjetsa mazunzo awo atsopano pokhulupilira kuti madalitso onsewa amene Mulungu anawatsapa ndi choonadi chao. Ndipo pakuti milili ya nthawi za mapeto ikutha kwa kanthawi kochepa, ndipo pakuti Mulungu adzapatsanso oyera Ake njira zoithawira, tonse tingapilire muimeneyo. Ndikhulupilira kuti, kuchokera pa nthawi imeneyi mpaka kutsogolo, mutalowa kale Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi ndi kukhala mu ufumu wa chikhulupiliro. 

Mu ufumu wa chikhulupiliro, onse mawuwa afunika kukhudza mtima wanu kupitila muchikhulupiliro, kutsiyana ndi chikhumba cha thupi lanu. Ngati yachita tero, mtima yanu idzakhala yolimba pamene ili kupedza mphamvu za tsopano, ndiponso idzakhala ndi chiyembekezo. 

Oyera onse adzaphedwa mnthawi za mapeto. Kuyangana pa chiyembekezo cimene tinaika Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi, ndife opitila pakulora kuphedwa mwa mphamvu zobwezeramo. 

Mu uzimu Wake, Ambuye Mulungu ndi Mulungu wa choonadi ndiponso Mulungu wachikondi. Kodi, ndiyeno, ndi anthu othani amene ndi amantha pamaso pa Mulungu? Awa ndi amene anabadwa ndi uchimo ndipo sanasukidwe ku machimo awo onse ndi uthenga wa madzi ndi Mzimu wopatsidwa ndi Ambuye. Cifukwa mzimu yawo ikupembeza oipa koposa mmene iwo akupembezera Mulungu, poyerayera akhala atumiki a Satana. Ndi cifukwa chakuti iwo akupembeza oipa pamaso pa Mulungu, ndiponso cifukwa iwo akukonda ndi kusata mdima kwambiri koposa kuwala, kotero kuti iwo ali n’mantha pamaso pa Ambuye Mulungu. Onse ali n’mantha pamaso pa Mulungu adzatenga mbali mnyanja yoyaka moto ndi sulufule. 

N’choona chokhazikitsidwa kuti anthuwa, amene pa iwo okha ndi mdima cifukwa cha machimo awo mmtimima yawo, alibe kusankha kwaina kulikonse koma kuoopa Mulungu. Monga miyoyo ya aja amene ndi a Satana ikonda mdima, iwo ndi amantha pamaso pa Yesu amene akhala kuwala. Ichi ndicho cifukwa iwo ayenera kupereka zoipa ndi kufooka kwawo kwa Mulungu ndi kulandira chikhululukiro cha machimo awo kuchokera kwa Iye. Onse amene sakhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu wopatsidwa ndi Ambuye ndi ochimwa aakulu pamaso pa Mulungu ndiponso ndi adani Ake. 

Monga mmene miyoyo yawo ndiyonyasa, ndipo cifukwa iwo asusana ndi Mulungu, chikondi ndi kuchita uchimo uliwonse umene uliko, akusata zidzindikiro zachinyengo, akupembeza mtundu uliwonse wa mafano, ndiponso akulankhula mtundu uliwonse wa maboza, mwa chiweruzo cholungama cha Mulungu onse adzaponyedwa mnyanja yoyaka moto ndi sulufule. Ichi n’chilungo chao cha imfa yachiwiri. 

Imfa yachiwiri idzaperekedwa ku anthu amene adzatumidwa ku gehena, ndipo awa ndi amene ali n’mantha, amene sakhulupilira, amene ndi onyansa, amene ndi akupha anthu, adama, achita za ulosi, ndiponso adama, amene, limodzi ndi Wosusa Khristu ndi omusatira ake, samvomera chikondi cha Mulungu tsopano. Amene sakhulupilira mwa Iye ndi oipitsitsa kwambiri. Baibulo limatiuza kuti onse oipawa ndi amene adzaponyedwa mnyanja yoyaka moto ndi sulufule. Ichi n’cifukwa Baibulo imati ndi imfa yachiwiri. 

Onse amene otengako mbali mchiukitso chachiwiri sadzafa ngakhale kuti adzaponyedwa mmoto, ndipo cifukwa cha cholinga chimenechi cha kuponyedwa mmoto, iwo adzaukitsidwa n’mathupi amene adzakhala moyo kwa muyaya. 

Osakhulupilira mwa Mulungu adzaukitsidwanso kuti aponyedwe mnyanja ya moto ndi sulufule. Chiukitso chachiwiri, cimene chidzabweretsa kuzunzidwa kosatha mmoto wa gehena kosafa, kusungidwira anthu onsewa amene sakhulupilira. 

Posatchedwa pambuyo pothira mbale 7 zokhala ndi milili 7, Ufumu wa zaka Chikwi chimodzi udzakwanilitsidwa, ndipo ngati zaka zake chikwi zapita, oyera adzankha Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi. Mmawu akuti, “Ndidzakuonetsani mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa,” mkazi wa Mwanawankhosa apa aimilira onse amene anapulumutsidwa ndi uthenga wa madzi ndi Mzimu wopatsidwa ndi Yesu Khristu ndiponso mwa kukhulupilira mu iwo. Ulemerero ndi Kukongola kwa Mzinda Woyera ndi Kosaneneka


Mzinda wa Yerusalemu umilira Mzinda Woyera kumene oyera adzakhala ndi Mkwati wawo. Mzindau umene Yohane anaona unalidi okongola ndiponso wabwino. Unali waukulu mmkula kwake, okongoletsedwa ndi miyala ya mtengo wapatali mkati mwake ndi kunja komwe, ocherezedwa ndiponso owala. Mngelo anamuonetsa Yohane kumene Akwatibwi a Yesu Khristu adzakhala ndi Mkwati wawo. 

Ganizani kukhala mnyumba ya chifumu yomangidwa ndi miyala ya mtengo wapatali. Mu Mzindau omangidwa ndi miyala 12 ya mitundu yosiyanasiyana, onse amene adzakhala akwatibwi a Mwanawankhosa adzakhala moyo kwa muyaya. Mzindau ndi mphatso ya Mulungu imene Iye adzaika pa mkazi wa Mwanawankhosa. Ndime imatiuza kuti mzinda wa Yerusalemu umawala mbee, ndi kuti kuwala kwake kuli ngati miyala ya mtengo wapatali kwambiri, ngati mwala wa yasipi, owala bwino ngati galasi. 

Ulemerero wa Mulungu choncho Mzinda ndi onse amene okhala mmenemo. Malo a Mulungu ndi akuwala, ndipo choncho ndi okhawo amene anayeretsedwa kuchoka ku mdima wawo onse, kuzofooka ndi kumachimo angalowe mu Mzindawo ndi kukhala mmenemo. Choncho, kuti tilowe mu Mzindawo Woyera, tonse tiyenera kukhulupilira mu Mawu oona okha a uthenga wa madzi ndi Mzimu umene Ambuye athu anatipatsa. 

Ndime ikuti Mzinda uli ndi mpanda waukulu ndiponso wautali ndi zipata 12. Ndiponso ikuti pa zipata maina analembedwapo, ndi kuti awa ndi maina a mafuko 12 a ana a Israeli. Mulungu amatiuza kuti Iye anakonzadi ndi kukonzeratu Mzindawo kukhala wa oyera Ake, ozungulilidwa ndi mpanda waukulu ndiponso wautali. 

Ichi ndi choonetsero cha kuuzimu kuti njira yolowera mu Mzindawu Woyera ndi yobvuta kwambiri. Chimatiuza kuti, mmawu ena, kupulumutsidwa kuchoka kumachimo anthu onse pamaso pa Mulungu n’chosatheka ndi mphamvu za umunthu kapena zinthu za katundu za dziko za chilengedwe cha Mulungu. Kuti tiomboledwe kuchoka kumachimo anthu onse ndi kulowa mu Mzinda Woyera wa Mulungu, n’kofunikira kwambiri kuti tonse takhala n’chikhulupiliro chimodzi cha ophunzira 12 a Yesu, chikhulupiliro cimene chikukhulupilira choonadi cha uthenga wsa madzi wa ndi Mzimu. Choncho, kulibe wina aliyense amene alibe chikhuylupilirochi mu uthenga wa madzi ndi Mzimu angalowe mu Mzindawu Woyera. 

Mzinda amatetezedwa ndi angelo 12 kuimilira ngati alonda a zipata osankhidwa ndi Ambuye Mulungu. Mawu akuti, “maina olembedwa pa izo [zipata],” kumbali ina, amatiuza kuti eni ake a Mzindawo anasankhidwa kale, pakuti eni ake ndi Mulungu Iyeyekha ndi anthu Ake, ndipo Mzinda ndi wa anthu Anthu amene tsopano nakhala ana Ake. 

Mzindawu Woyera uli ndi zipata zitatu kumbali zake zinayi ku kumpoto, kumwera, kumvama, ndi kumadzulo. Ndi kukhulupilira kuti Ambuye makamaka anatchula zipata zitatuzi apa amatiuza kuti izo zikugwirazana ndi uthenga umene timakhulupiliramo. 1 Yohane 5:7-8 ikunena kuti pali zitatu zimene zikuchitira umboni uthenga woona limodzi Kumwamba ndi pa dziko lapansi. Ndi okhawo amene okhulupilira mu mbonizi zitatu, limodzi Kumwamba ndi pa Dziko lapansi, angalowe Kumwamba. Ife, obadwa-mwatsopano, tikhulupilira mu Mulungu Mutatu ndi mu nchito Zake za chilungamo zotipulumutsa kupitila mu madzi, magazi, ndi mu Mzimu. 

Choona chakuti maina a atumwi 12 analembedwa pa maziko a mpanda wa Mzinda chikutiuza kuti Ambuye anachita mmene Iye analonjezera, kuti Iye sadzafafaniza maina awo kuchoka mu Buku la Moyo koma kuwalemba mmenemo.

Masitadiya, ‘Stadion’ mu Chigiriki, ndi unyinji wa kayezero ka mtunda, okwana 600 futu (185 m) mkayezero ka matsiku ano. Pamene Baibulo limatiuza kuti mbali iliyonse ya Mzinda Kumwamba ndi okwanira masitadiya 12, 000, imatiuza kuti mbali ina iliyonse ikwanira makilomita 2,220 (1,390 miles). Tikuuzidwanso kuti m’litali mwake, m’lifupi, ndiponso msinkhu mwake n’zofanana. Kukula kwa Mzindakukutiuza za mmene kulili kukula ndi ulemerero wa Ufumu wa Mulungu. 

Tanthauzo la baibulo la nambala ndi kuzunzidwa. Chikhulupiliro cimene Ambuye akufuna kwa ife si chinthu cimene aliyense angakhala nacho, koma chikhulupilirochi angakhale nacho ndi okhawo amene akumvomera Mawu a Mulungu mmene alili, nkhale kuti sangayakwani onse, ndi maganizo awo awo opangidwa-ndi munthu. 

Monga Akristu, ndichosatheka kulowa mu Mzinda Woyera wa Mulungu pokhulupilira mu Mtanda wa Yesu wokha, ndi kuti Ambuye ndi Mulungu ndiponso M’pulumutsi. Monga mmene Ambuye Iyeyeka analankhula, kulibe wina aliyuense amene angalowe mu Ufumu wa Mulungu pokhapo iye wa badwa-mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu. Anthu angabadwe mwatsopano pokhapo ngati okhulupilira kuti machimo onse adziko lapansi anaikidwa pa Yesu pamene Iye anali atabatizidwa ndi Yohane M’batizi, ndi kuti Iye anapepetsa machimo pokhetsa magazi Ake ndi kufa pa Mtanda mmalo mwao. 

Mawu akuti, “mzinda unali golide wonyezimira, ngati kuwala kwa galasi,” amatiuza kuti ndi okhawo amene chikhulupiliro chao chili ngati golide—amene ndi, okhawo okhulupiliradi mwa Mulungu—angalowe mmenemo. Amatiuza kuti chikhulupiliro cimene chimalora wina kuti alowe mu Mzinda Woyera wa Ambuye ndi mtundu wa chikhulupiliro cimene chikukhulupilira mu Mawu a Mulungu mmene analembedwera, cimene n’choyera ndiponso chomasuka kuchoka ku zinthu za dziko. Amatiuza, mmawu ena, kuti wina ayenera kumvomereza Mawu a Mulungu a kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu mu chiyero chake, kukhulupiliradi mu Mawuwa, ndipo chikhulupiliro chake chikhale choyengedwa. 

Maziko a mpanda wa Mzinda ndi okongoletsedwa ndi mtundu uliwonse wa miyala ya mitengo wapatali, kutiuza kuti tingacherezedwa mu zikhulupiliro zotsiyana tsiyana kuchokera mu Mawu a Ambuye athu. Tiyenera kukhala ndi chikhulupiliro cha khalidwe labwino, osati chikhulupiliro chabe mu uthenga wa madzi ndi Mzimu kapena chiyembekezo cha Kumwamba ndi Ufumu wa zaka Chikwi chimodzi. Ichi chikhulupiliro chiphunzitsidwa chimachokeranso kupitila mu Mawu a Mulungu pamene tikupilira mu mazunzo a matsiku ano. 

Ambuye anapatsa oyera osati dalitso Lake lokha la khululukidwa machimo awo, komanso dalitso la kukwanilitsa chiyembekezo chao, kuti onse amene okhululukidwa machimo awo adzalowa mu Ufumu wa zaka Chikwi chimodzi ndi Kumwamba. If oyera tingathokoze Mulungu kokha potikwanilitsa kuti tilowe Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi, kumene sikupezekanso nkhawa kapena chisoni. 

Oyera amene adzalowa mu Mzinda Woyera afunika kukhala odekha mtima kwambiri pamene akalibe padzikoli lapansi, kuima njii pakati pa chikhulupiliro chao. Onse amene okhulupilira mu Mawu a choonadi olankhulidwa ndi Ambuye Mulungu, mmawu ena, afunika kukhala ndi chipiliro chachikulu kuti ateteze chikhulupiliro chao. Ngati nthawi yamapeto yabwera, nthawi ya Wosusa Khristu, mdani wa chikhulupiliro, adzabwera. 

Wosusa Khristuyu, ngati mtumiki wa Satanma, adzabweretsa mazunzo ku anthu ambiri achikhulupiliro, kufunafuna kuti awapange iwo kupandukira chikhulupiliro chao. Ngati anthu akhala mbali ya Wosusa Khristu ndi kutataya chikhulupiliro chao, osati Ufumu wa zaka Chikwi okha ndi Kumwamba kwa tsopano udzakhala kutali kuti iwo afikeko, koma iwo adzaponyedwanso mgehena limodzi ndi Satana.

Choncho, pakati pa mayetsero, mazunzo, ndi milili ya nthawi za mapeto, tonse tidzafunika chipiliro cimene chidzatilowa kuti titeteze chikhulupiliro chathu molimbika, pakuti chikhulupilirochi chosagwendezeka ndi cimene chidzapanga kuti Kumwamba kwa Tsopanondi Dziko lapansi zikhale zathu. 

Kukhala Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi kuli ngati kukhala olandilidwa mu manja a Ambuye. Pakuti Yesu Khristu amene anakhala kuwala kwa dziko la tsopano, akuwala mdzikoli loyera ngati kuwala kwake, kumeneko sikufunikanso dzuwa kapena mwezi ku uwale kumeneko. Yesu Khristu ndi M’pulumutsi wathu, Mlingi, ndiponso Mweruzi, ndipo Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi Iye ndi Mulungu amene okhala nndi ife. Mwa Iye tikulowa Kumwamba, ndiponso kuchokera kwa Iye madalitso onse akusefukira. Oyera adzakhala alibe china chilichonse koma tsiku ndi tsiku kumayamikira Ambuyeyu. 

Mu King James Version, ndime 24 analembedwa ngati zosatirazi: “Mitundu ya anthu idzayenda mwa kuwala kwake, ndipo mafumu a dziko lapansi adzabweretsa ulemerero wawo mumzindawo.” Pamene ikunena apa kuti ulemerero wa dziko lapansi udzabweretsedwa Kumwamba, ichi si chitanthauza kuti amene anakhala padziko lapansi loyamba, pakuti anali achuma, adzabweretsa chuma chao Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi. Dziko lapansi apa likuimilira Ufumu wa zaka Chikwi chimodzi. 

Ngakhale kuti oyera opulumutsidwa ndipo adzalowa mu Ufumu wa zaka Chikwi chimodzi onse mnjira imodzi, iwo adzapatsidwa ulamuliro otsiyana, ena kulamulira pa mizinda 10 ndiponso enanso pa mizinda isanu, malinga ndi mmene iwo anali kulikira uthenga pamene anali kukhala mdziko loyamba. 

Cimene ndime ya 24 imatiuza apa ndikuti mafumuwa amene anali ndi ulamuliro otsiya tsiyana adzapita Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi. Amene anakhalamo mu Ufumu wa zaka Chikwi chimodzi, mmawu ena, adzalowa Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi ngati mafumu limodzi kubweretsa chikhulupiliro chao mwa Ambuye ndi ulemerero wao wonse ndi ulemu. Choncho chilibe ndi chochita ndi dzikoli lapansi loyamba mmene onse aife tilikukhala tsopano. 

Pakuti Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi, kumene Mzinda Woyera unakhazikitsidwa, kunadzala kale ndi kuwala koyera, kumeneko si kungakhale usiku, kapena choipa china chilichonse. Pakati pa onse Akristu ndi amene Si-Akristu a dzikoli chimodzimodzi, onse amene sakudziwa choonadi cha uthenga wa madzi ndi Mzimu ndi odetsa, onyansa, ndiponso aboza. Iwo choncho sangalowe mu Mzinda Woyera. Pakuti aliyense amene okhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu angalowe Kumwamba, uthengawu wa madzi ndi Mzimu ndi kiyi wa Kumwamba ndiponso kiyi wa chikhululukiro cha uchimo. Muyenera kudzindikira kuti ngati mwadzindikira ndiponso kukhulupilira kuti Mulungu anamupatsani kiyiyu, dzina lanu lidzalembedwa mu Buku la Moyo. Ndipo ngati mwamvomera choonadi cha uthenga, mdzabvekedwa dalitso lolowera mu Mzinda Woyerawu. 

Khulupilirani kuti Mzinda Woyera wunapatsidwa kale kwa ife. Ndipo khalani moyo wanu malingana, ndi chiyembekezo. 

Cifukwa zinthu zonse zimene tikukumana nazo pa nthawi imene tilipo zikuyezedwa ndi kulemera kwa chikonzedwe cha katundu wa dziko, sitinganenedi kuti cimene ndi chikondwerero choona. Koma ngati tayeza ndi ndodo yoyezera ya Mulungu, tingadzindikire kuti amene ali N’kumwamba pa katundu umene iwo alinawo ndi okondwera oona. Cifukwa nciani? Cifukwa posachedwa kapena chatsopanopa, zinthu za dziko zonse zidzazimiririka. Kukhala kopanda malo poika chiyembekezo chathu, zonse zidzazimirirka pamene masautso ndi milili idzabweretsedwa pomalizira pake, malingana ndi chikonzero cha Mulungu. Kulibe china chilichonse cimene n’choputsa kwambiri kopotsa kuika chiyembekezo cha wina mu zinthu zotero za thupi zimene zidzawola ndi kutenthedwa kukhala phulutsa. 

Koma motsiyanitsa, onse amene oika chiyembekezo chao mu Ufumu osatha wa Kumwamba umene sidzawola kapena kutenthedwa ndi odala. Ndi okhawo amene alibe uchimo angalowe Mzinda Woyera wa Yerusalemu okonzedwa ndi Mulungu. Anthu okondwera kwambiri mdzikoli lapansi ndi amene ali N’kumwamba pa katundu yawo, amene machimo onse ana khululukidwa ndipo anasukidwa. 

Tiyenera kukhala miyoyo yathu yodalitsidwa ndi Mulungu, monga amene akupereka ulemerero kwa Iye cifukwa chotipatsa Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi, ndi amene odzipereka ife tokha pakulalika uthenga oona umene ukulora wina aliyense ndiponso moyo uliwonse kulowa Kumwamba. 

Tiyeni tonse tikhale mdalitso lotero, tiyeni tikondedwe ndi Mulungu, ndipo, ngati tiima pamaso pa Ambuye wathu, tiyeni tonse tikhale olandilidwa kwa muyaya mumanja Ake.