Sermons

[22-1] < Chivumbulutso 22:1-21 > Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi, Kumene Madzi a Moyo Akusefukira< Chivumbulutso 22:1-21 >

“Ndipo anandionetsa mtsinje wa madzi a moyo, oyera ngati mwala wonyezimira wa kulusitalo, ukuyenda kuchokera kumpando wachifumu wa Mulungu, ndi wa Mwanawankhosa. Mtsinjewo unali kudutsa pakati pamsewu waukulu wa mumzindawo. Kumbali iyi ya mtsinjewo ndi kumbali inayo, kunali mitengo ya moyo yobala zipatso zokolola maulendo 12, ndipo inali kubala zipatso mwezi uliwonse. Masamba a mitengoyo anali ochiritsira mitundu ya anthu. Sikudzakhalanso temberero. Koma mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa udzakhala mumzindamo, ndipo akapolo a Mulungu adzachita utumiki wopatulikao kwa iye. Iwo adzaona nkhope yake, ndipo dzina lake lidzakhala pamphumi pawo. Komanso, usiku sudzakhalakonso. Sadzafunikiranso kuwala kwa nyale kapena kwa dzuwa, chifukwaYehova Mulungu adzawaunikira. Ndipo adzalamulira monga mafumu kwamuyaya. Kenako anandiuza kuti: “Mawu awa ndi odalirika ndiponso oona. Yehova, Mulungu wopereka mauthenga ouziridwa a aneneri, anatumiza mngelo wake kudzaonetsa akapolo ake zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwa. Ndipo taonani! Ndikubwera mofulumira. Wodala ndi aliyense wosunga mawu a ulosi mumpukutu uwu.” Ine Yohane, ndine amene ndinali kumva ndi kuona zinthu zimenezi. Ndipo nditamva ndi kuona, ndinagwada n’kuwerama kuti ndilambired pamapazi a mngelo amene anali kundionetsa zinthu zimenezi. Koma iye anandiuza kuti: “Samala! Usatero ayi! Inetu ndangokhala kapolo mnzako, ndi wa abale ako amene ndiwo aneneri, ndi wa anthu amene akusunga mawu amumpukutu umenewu. Lambira Mulungu.” Anandiuzanso kuti: “Usatsekere mawu a ulosi a mumpukutu uwu, pakuti nthawi yoikidwiratu yayandikira. Amene akuchita zosalungama, achitebe zosalungama, ndipo wochita zonyansa apitirizebe kuchita zonyansazo. Koma wolungama achitebe chilungamo, ndipo woyera apitirizebe kuyeretsedwa. ‘Taonani! Ndikubwera mofulumira, ndipo mphoto ndili nayo, yoti ndipereke kwa aliyense malinga ndi ntchito yake. Ine ndine Alefa ndi Omega, woyamba ndi wotsiriza, chiyambi ndi mapeto. Odala ndiwo amene achapa mikanjo yawo, kuti akhale ndi ufulu wa kudya zipatso za m’mitengo ya moyo, ndiponso kuti akalowe mumzindawo kudzera pazipata zake. Kunja kuli anthu amene ali ngati agalu, amene amachita zamizimu, adama, opha anthu, opembedza mafano, ndi aliyense wokonda kulankhula ndi kuchita zachinyengo.’ ‘Ine Yesu, ndinatumiza mngelo wanga kudzachitira umboni zinthu izi kwa inu, kuti zithandize mipingo. Ine ndine muzu ndi mbadwa ya Davide. Ndinenso nthanda yonyezimira.’ Mzimu ndi mkwatibwi akunenabe kuti: “Bwera!” Aliyense wakumva anene kuti: “Bwera!” Aliyense wakumva ludzu abwere. Aliyense amene akufuna, amwe madzi a moyo kwaulere. “Ine ndikuchitira umboni kwa aliyense wakumva mawu a ulosi wa mumpukutuwu, kuti: Wina akawonjezera pa zimenezi, Mulungu adzamuwonjezera miliri yolembedwa mumpukutuwu. Ndipo wina akachotsa kalikonse pa mawu a mumpukutu wa ulosi umenewu, Mulungu adzachotsa gawo lake pa zolembedwa mumpukutuwu, kutanthauza kuti sadzamulola kudya zipatso za m’mitengo ya moyo, ndipo sadzamulola kulowa mumzinda woyerawo. ‘Amene akuchitira umboni zinthu zimenezi akuti, ‘Inde, ndikubwera mofulumira.’ “Ame! Bwerani, Ambuye Yesu.” Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu Khristu kukhale ndi oyerawo.’”Kusanthula 


Ndime ya 1: Ndipo anandionetsa mtsinje wa madzi a moyo, oyera ngati mwala wonyezimira wa kulusitalo, ukuyenda kuchokera kumpando wachifumu wa Mulungu, ndi wa Mwanawankhosa. 

Apa ikuti Yohane anaonetsedwa, “mtsinje wa madzi, oyera ngati mwala wonyezimira wa kulusitalo.” Mawu akuti madzi amagwiritsidwa nchito madzikoli ngati chimodzimodzi ndi moyo. Ndime apa ikuutiza kuti madziwa a moyo akusefukira Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi kumene oyera adzkhala kwa muyaya. Kusefukira kuchoka ku mpanda wachifumu wa Mwanawankhosa, mtsinje wa moyo ukunanitsa Ufumu wa Kumwamba ndi kubwezeramo zinthu zonse. Mu mawu akuti, “mpando wachifumu wa Mwanawankhosa,” “Mwanawankhosa” aimilira Yesu Khristu, amene anapulumutsa anthu mwa uthenga wa madzi ndi Mzimu pamene anali padziko lapansi. 

Kumwamba ndi Dziko lapansi limene Mulungu anapereka ku oyera Ake, madzi a moyo akusefukira. Pakuti mundawu ndi oyera ndipo oyera ngati madzi okongola a mtundu opentera, angatchulidwe kuti ndi abwino. Madzi a moyo amene Mulungu anatipatsa sin’mtsinje wamba, koma ndi madzi amene amapatsa moyo ku zinthu zonse za moyo kumeneko. Choncho, moyo udalira mu zinthu zilizonse zimene zikugwirizana ndi mtsinjewu wa moyo. Oyera amene afuna kukhala mmbali mwa mtsinje wa madziwa a moyo adzamwa madziwa, kusangalala moyo osatha ndi kukhala kwa muyaya. 

Mtsinje wa madzi a moyo akusefukira kuchokera kumpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa. Oyera sangaleke koma kumayamika chisomo cha Mulungu ndiponso cha Mwanawankhosa mu Ufumu wa Tsopano wa Kumwamba, pakuti Mulungu anaika paiwo chisomo Chake cha moyo. Ndine othokoza kuti chisomo chonse cha moyowu wa tsopano chikusefukira kuchokera kumpando wa Ambuye. 


Ndime ya 2: Mtsinjewo unali kudutsa pakati pamsewu waukulu wa mumzindawo. Kumbali iyi ya mtsinjewo ndi kumbali inayo, kunali mitengo ya moyo yobala zipatso zokolola maulendo 12, ndipo inali kubala zipatso mwezi uliwonse. Masamba a mitengoyo anali ochiritsira mitundu ya anthu. 

Msewu wa madalitso a Ambuye pa oyera Ake Kumwamba upitiliza, pakuti Mawu akutiuza apa kuti Ambuye adzatipatsa mtengo wa moyo kumbali zonse za mtsinje ndi kutilora kudya kuchokera ku zipatso zake. Mtengo wa moyo, umene ukubala mitundu 12 ya zipatso, ukubala zipatso zake za tsopano mwezi uliwonse, kubweretsa nyonga ya moyo wa tsopano. Apa chanenedwanso kuti masamba ake ndi ochiritsa mitundu ya anthu. 

Cifukwa chisomo cimene Ambuye anaika pa oyera Ake n’chachikulu kwambiri ndiponso chothokozedwa kwakukulu, cimene ife tingachite chabe ndi kumuyamika Iye ndi Mulungu Atate. Tsopano, cimene oyera ayenera kuchita si kufuna kuchita cha mtengo wapatali kwa Ambuye pa iwo okha, koma mmalo mwake kumangoyamikira kokha Ambuye ndi mitima yawo yoyamikira powapatsa iwo Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi ndiponso moyo. Ndiyamika Ambuye popanga mitima ya oyera kumangofuula, “Zikomo inu, Ambuye! Haleluya!” 


Ndime ya 3: Sikudzakhalanso temberero. Koma mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa udzakhala mumzindamo, ndipo akapolo a Mulungu adzachita utumiki wopatulikao kwa iye. 

Ku oyera okhala mu Ufumu wa Kumwamba, Mulungu anapereka dalitso lochotsa temberero kwa muyaya. Kunena kuti mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa uli pakati pa oyera chimationetsa kuti oyera amene okhala mu Ufumu wa kumwamba ukuika Mwanawankhosa pakati pa mitima yawo. Choncho, mitima ya oyera tsiku ndi tsiku ikusefukira ndi kongola ndiponso choonadi, ndipo miyoyo yawo ndi yodzaza ndi cimwemwe. 

Kuchokera mu mawu akuti, “akapolo a Mulungu adzachita utumiki wopatulikao kwa Iye,” tikuona kuti oyera okhala mu Ufumu wa Kumwamba ndi obvekedwa mu ulemerero wakutumikira Ambuye pafupi kwambiri ndi Iye. Ufumu wa Kumwamba, kumene Ambuye okhala, ndi Ufumu okongola kwambiri ndiponso olemekezeka. 

Choncho, atumiki Ake amene akutumikira Iye pafupi ndi Ambuye adzanjoya mu ulemerero Wake wonse pafupi. Ichi chimatiuza kuti mu Ufumu wa Kumwamba nakonso, kudzakhalanso atumiki a Ambuye. Mawu akuti mtumiki aimilira kuzichepetsa, koma atumiki amene angatumikire Ambuye athu olemekezeka pafupi ndi Iye ndi odala koposa mu Ufumu wa Kumwamba nakonso, pakuti iwo obvekedwa mu ulemerero waukulu otero osaneneka. Onse amene akhala atumiki a Ambuye mu Ufumu wa Kumwamba ndi dzikoli lapansi naonso ndi amene adzabvekedwa mu ulemerero wonse wa kumwamba ndipo ndi amene osangalala kwambiri paonse. 


Ndime ya 4: Iwo adzaona nkhope yake, ndipo dzina lake lidzakhala pamphumi pawo. 

Kodi ndi kwa ndani kumene oyera onse ndi atumiki a Ambuye ayenerera? Ayenerera kwa Ambuye. Iwo ndi anthu a Ambuye ndiponso ana a Mulungu. onse amene akutumikira Ambuye mu Ufumu wa Kumwamba, choncho, ali ndi dzila la Ambuye lolembedwa pamphumi pawo. Tsiku ndi tsiku Ambuye amawateteza ndi kuwadalitsa, pakuti iwo akhala ana Ake. Kunena kuti oyera akhala Ake kutanthauza kuti akhala obvekedwa mmodzi mwa ulemero osangalatsa kwambiri ndiponso olemekezeka kwambiri. Onse amene akuchita manyazi cifukwa chokhala Ake ndi atumiki a Ambuye ndi aja amene sakudziwa za ulemerero Wake, ndipo sangakhale eni ake a Kumwamba. 

Pamphumi pa oyera okhala Kumwamba, dzina la Ambuye linalembedwapo. Ili ndi dalitso loikidwa ndi Ambuye. Kuchokera tsopanoli, oyera akhala Ake. Choncho, ngakhale Satana sangapweteke oyera amene akhala a Ambuye. Oyera ndi Ambuye adzakhala limodzi mu ulemerero onse wa Kumwamba. Kunena kuti oyera adzaona nkhope yolemekezeka ya Ambuye tsiku ndi tsiku chitanthauza kuti adzakhala chikondi Chake ndiponso madalitso odabwitsa kwamuyaya.

Kulinso chinthu chimodzi cimene oyera afunika kuchidziwa: Limodzi ndi Ambuye Yesu, Mulungu Atate ndi Mzimu Woyera naonso wudzakhala ndi iwo ngati banja lawo. Sityenera kuyaiwala kuti mu Ufumu wa Kumwamba, Mulungu Atate, Mwana Wake Yesu, Mzimu Woyera, oyera, ndiponso angelo ndi zinthu zonse adzakhala limodzi ngati banja limodzi ndiponso mu ufulu wokomela aliyense. Ndiyamika Ambuye potipanga kukhala Ake. 


Ndime ya 5: Komanso, usiku sudzakhalakonso. Sadzafunikiranso kuwala kwa nyale kapena kwa dzuwa, chifukwaYehova Mulungu adzawaunikira. Ndipo adzalamulira monga mafumu kwamuyaya. 

Monga mmene Baibulo imatiuzura apa, oyera adzalamulira Kumwamba kwa tsopano ndi Dziko lapansi limodzi ndi Ambuye. Onse amene akhala oyera Ake pokhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu analandila chipulumutso cimene chidzawalora kulamulira Kumwamba limodzi ndi Ambuye ndi kukhala mchuma Chake, ulemerero ndi ulamulira kwamuyaya. Ndife odabwanso ndi uthengau, pakuti uthenga wa mphamvu yodabwitsa ndi dalitso tilinawo! 

Ndiyamika Mulungu wathu wa Utatu cifukwa cha madalitso onsewa ndi ulemerero. Oyera amene nakhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu pamene anali padziko lapansi adzalamulira mu Ufumu wa Kumwamba. Ndi dalitso lodabwitsa kotani! Sitingaleke koma kumayamikira Ambuye. Ndi choyenerera ndipo chofunika kuti kutero iwo ayenera kumayamika Mulungu. 

Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi kumene oyera okhala, sikufunikanso nyale, maglobo amagesi, kapena dzuwa. Cifukwa nciani? Cifukwa Mulungu Iyeyekha akhala kuwala kwa Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi, ndipo kumeneko sikudzakhalanso usiku. Mulungu walora oyera kuti alamulira mmenemo ngati ana Ake kwamuyaya. Dalitso limatikumbatsanso mmene chilili kukulu chisomo cimene oyera analandira kuchokera kwa Ambuye. 

Ife oyera tiyenera kudzindikira mmene alili kukula madalitso a Kumwamba oikidwa pa ife pambuyo pa chipulumutso chathu. Chisomo cimene Ambuye athu anaika pa oyera Ake n’chachitali ndiponso chachikulu koposa mtambo. Oyera safunika kulora dalitsoli lodabwitsa limene Ambuye anawapatsa kupitilira. Oyera angapereke chabe mathokozo osatha ndiponso mayamiko ku Ambuye cifukwa cha ukulu Wake, ulemerero, ndi dalitso limene inaika pa iwo, ndi kukhala mchuma ndi ulemerero kwamuyaya. Ameni! Haleyuya! Ndiyamika Mulungu wathu!


Ndime ya 6: Kenako anandiuza kuti: “Mawu awa ndi odalirika ndiponso oona.” Yehova, Mulungu wopereka mauthenga ouziridwa a aneneri, anatumiza mngelo wake kudzaonetsa akapolo ake zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwa. 

“Mawu awa ndi odalirika ndiponso oona.” Ambuye adzakwanilitsadi malonjezo Ake amene Iye anawavumbulkutsa ku oyera kupitila mu Chivumbulutso. Ichi ndicho cifukwa Ambuye athu anavumbulutsa zinthu zonse ku oyera Ake nthawi isanabwere kulankhula ngati Mzimu Woyera kupitila mu atumiki a Mulungu. Kodi ndi Mawu otani amene ndi odala kwambiri mu Buku la Chivumbulutso? Muli Mawu odala ambiri mu Chivumbulutso, koma Mawu odala kwambiri ndi akuti Mulungu adzalora oyera kulamulira limodzi ndi Ambuye Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi ndi kukhala mu ulamuliro ndiponso ulemerero. 

Pakuti Mulungu adzakwanilitsadi nchitoyi posachedwapa, oyera sangalore chikhulupiliron chao kuti chipwanyike kapena chigwere muchionongeko. Oyera afunika kugonjetsa mayetsero onse ndi masauso ndi chikhulupiliro chao cha chiyembekezo. Ambuye ethu sadzalephera kupanga maulosi ndi malonjezo Ake amene analonjeza ku oyera ndiponso ku M’pingo wa Mulungu kuchitika. Ambuye athu anatumiza atumiki Ake padzikoli lapansi ndi kuwapanga kuti alankhule Mawu aulosi, kotero kuti Iye auze oyera Ake ndi M’pingo za madalitso onsewa. 


Ndime ya 7: “Ndipo taonani! Ndikubwera mofulumira. Wodala ndi aliyense wosunga mawu a ulosi mumpukutu uwu.”

Pakuti Mawu aulosi a mu Bukuli la Chivumbulutso amatiuza za kuphedwa kwa oyera kwakutsogolo, amavumbulutsa kwa ife kuti nthawi idzabwera pamene oyera adzazunzidwa ndi Wosusa Khristu ndipo ayenera kuteteza chikhulupiliro chao mpaka kufa. Pakuti n’chifuniro cha Mulungu, oyera ayenera kulora kuphedwa kwao. Iwo ndiyeno adzatengako mbali mchiukitso chao ndi kwatulidwa, adzalamulira mu Ufumu wa Khristu kwa zaka chikwi chimodzi zikubwera, ndi pamene adzakhala Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi kwa muyaya. Choncho, oyera afunika kukhulupilira mu Mawu onse a Mulungu amene Ambuye athu analakhulu kwa iwo ndi kusunga chikhulupiliro chao. Odala kwambiri a nthawi za mapeto ndi aja amene okhulupilira mu Mawu a Ambuye athu ndi kukhala moyo mwa chikhulupiliro. 

Mulungu anauza oyera Ake kuti Iye adzabwera mofulumira. Ambuye adzabwera kwa ife kosachedwa kulikonse. Kuti adzakwanilitse madalitso onse a Mulungu oyenda kuchokera mu Mawu a madzi ndi Mzimu, Mawu amene amabweretsa ku oyera chipulumutso chao kuchoka ku uchimo, Ambuye athu adzabwera padzikoli lapansi mofulumira. 

Atapulumutsidwa, oyera ayenera kugwililira ku Mawu a madalitso a Ambuye olonjezedwa ku iwo, ndi kusunga chikhulupiliro chao. Ngati mitima yawo yataya chikhulupiliro chao mu Mawu a Ambuye, adzataya zinthu zonse, ndipo ichi ndicho cifukwa ayenera kuteteza chikhulupiliro chao mu Mawu a Ambuye. Mulungu amauza oyera, mmawu ena, kuti asunge chikhulupiliro chao mwa Ambuye. 


Ndime ya 8: Ine Yohane, ndine amene ndinali kumva ndi kuona zinthu zimenezi. Ndipo nditamva ndi kuona, ndinagwada n’kuwerama kuti ndilambired pamapazi a mngelo amene anali kundionetsa zinthu zimenezi. 

Ndi aneneri ndiponso oyera amene amafalitsa Mawu aulosi a Mulungu. choncho tiyenera kuyamikira Mulungu amene akugwiria nchito mmene Iye analankhulira ku iwo, ndipo tiyenera kupembeza Iyeyekha. Nthawi zina anthu ena amafuna kuzikwezeka okha pamwamba ngati Mulungu ndi kuwatenga momwemo. Iwo akuchita tero cifukwa iwo mwina ndi anyenga kapenda aneneri achinyengo. Ndi Mulungu yekha amene ndi oyenerera kulandira mayamiko onse, matamando, ulemerero, ndiponso kubwezerapo. 


Ndime ya 9: Koma iye anandiuza kuti: “Samala! Usatero ayi! Inetu ndangokhala kapolo mnzako, ndi wa abale ako amene ndiwo aneneri, ndi wa anthu amene akusunga mawu amumpukutu umenewu. Lambira Mulungu.” 

Kodi tiyenera kuchita nciani kuti tikhala aneneri a Mulungu oona? Poyamba tiyenera kukhulupilira mu chinsinsi cha uthenga wa madzi ndi Mzimu wopatsidwa ndi Ambuye. Ndiyeno tidzakhala anthu a Mulungu, oyera, ndiponso abale ndi alongo ku wina ndi mzache. Ndi pokhapo chitapita ichi n’pamene Mulungu agawagamure ndi ntchito Zake. Onse amene akhala atumiki a Ambuye pokhulupilira mu Mawu Ake ndi kuyasunga mwa chikhulupiliro chao. Awa ndi amene amapereka ulemerero wonse kwa Mulungu mmalo mozisungira iwo okha. Ambuye athu ndi oyenerera kulandira matamando ndi ulemerero kuchokera ku wina aliyense mdzikoli lapansi. Haleluya!


Ndime ya 10: Anandiuzanso kuti: “Usatsekere mawu a ulosi a mumpukutu uwu, pakuti nthawi yoikidwiratu yayandikira.”

Mawu a lonjezo olembedwa mu Chivumbulutso si ayenera kusungidwa mobisika. Cifukwa adzakwanilitsidwa posachedwapa, ayenera kuchitilidwa umboni ndi wina aliyense. Ameni!, tiyeni tonse tikhulupilire mu Mawu aulosi a mu Buku la Chivumbulutso ndi kuwalalikira. 


Ndime ya 11: “Amene akuchita zosalungama, achitebe zosalungama, ndipo wochita zonyansa apitirizebe kuchita zonyansazo. Koma wolungama achitebe chilungamo, ndipo woyera apitirizebe kuyeretsedwa.”

Ngati tsiku lobweranso Ambuye layandikira, Iye adzalora amene akufunafuna uchimo kuti apitirizebe kuchita uchimo, ndiponso onse amene ochita zonyansa kuti apitirizebe kukhala onyansa. Ngati nthawi yamapeto yabwera, onse amene mitima yawo yakhala yopanda uchimo pokhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu adzapitilizabe kutumikira uthenga padzikoli lapansi, ndipo onse amene asungilira chiyero chao chopatsidwa ndi Ambuye ndiponso anakhala miyoyo yawo mwa chikhulupiliro adzapitirizabe kukhala tero. Ambuye anthu amatilimbitsa kuti tisunge chikhulupiliro cimene tili nacho tsopanoli. 


Ndime ya 12: “Taonani! Ndikubwera mofulumira, ndipo mphoto ndili nayo, yoti ndipereke kwa aliyense malinga ndi ntchito yake.” 

Ambuye athu adzabwera posachedwa, mmawu ena, adzapereka Paradaiso padziko lapansi ndi Kumwamba kwa Tsopano ku oyera amene atumikira ndi kugwira nchito mwa mphamvu pofalitsa uthenga wa madzi ndi Mzimu, kuti awapatse mphoto cifukwa chozipereka kwao. Ngati oyera akhulupilira mu Mawu aulosi wa mu Chivumbulutso, iwo adzakwanitsa kuteteza chikhulupiliro chao mpaka pamapeto ake enieni, cifukwa iwo adzaika chiyembekezo chao mwa Ambuye. Tiyenera kudzindikira ndi kukhulupilira kuti Ambuye adzapereka mphoto pogwira nchito mwa mphamvu kwa oyera ndi madalitso aakulu kwambiri, pakuti Ambuye athu ndi olungama ndiponso achifundo. 


Ndime ya 13: “Ine ndine Alefa ndi Omega, woyamba ndi wotsiriza, chiyambi ndi mapeto.”

Ambuye athu ndi chiyambi ndi mapeto a zinthu zonse. Iye ndi M’pulumutsi wathu ndinso Mulungu Iyeyekha, amene adzabweretsa kutsilizitsa kwa chipulumutso chokha cimene Iye angatipatse. Mbiri yonse ya dziko lonse, mbiri ya Kumwamba ndi dziko lapansi, inachokera kwa Ambuye ndipo idzathetsedwa ndi Iye. 


Ndime ya 14: Odala ndiwo amene achapa mikanjo yawo, kuti akhale ndi ufulu wa kudya zipatso za m’mitengo ya moyo, ndiponso kuti akalowe mumzindawo kudzera pazipata zake. 

Pakuti zimene Ambuye analankhula kwa ife zonse ndi moyo, oyera okhulupilira mu Mawu Ake, akulalikira ndi kuwateteza. Akuchita tero cifukwa Mawu amene Ambuye athu analankhula ku oyera Ake ndi ku zinthu zonse mdziko lonse onse n’oona. Ichi ndicho cifukwa oyera ndi atumiki a Mulungu amasunga Mawu a Mulungu mmitima yawo. Amateteza chikhulkupiliro chao pokhulupilira mu Mawu a Mulungu ngakhalenso molimbika, kotero kuti akhale ndi ufulu wa kudya zipatso za mu mtengo wa moyo obyalidwa Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi. 

Oyera amene akhala opanda uchimo pokhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu wopatsidwa ndi Ambuye afuna kuteteza chikhulupiliro chao, cifukwa iwo ali ndi ufulu wa kudya zipatso za mtengowu wa moyo Kumwamba. 


Ndime ya 15: Kunja kuli anthu amene ali ngati agalu, amene amachita zamizimu, adama, opha anthu, opembedza mafano, ndi aliyense wokonda kulankhula ndi kuchita zachinyengo.

Onse otchulidwa pa ndime yapamwambapa ndi amene sakhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu, ndipo iwo choncho si obadwa mwatsopano ngakhale kufika mpaka ku nthawi za mapeto. Wosusa Khristu ndi omsatira ake, asocheretsa anthu ndi zidzindikiro zake ndiponso zodabwitsa, awasocheretsa tsiku ndi tsiku pakuchita chinyengo kunena kuti Wosusa Khristu ndi M’pulumutsi. Iwo atsogolera anthu kuchionongeko chao powapanga kuti apemembeze chifaniziro cha Wosusa Khristu. Ambuye athu amasunga anthu otero kunja kwa zipata za Mzinda Woyera, kotero kuti asalowe Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi. Mzinda wa Ambuye nditseguka ku oyera okha amene anateteza chikhulupiliro chao cimene chikhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu. 


Ndime ya 16: “Ine Yesu, ndinatumiza mngelo wanga kudzachitira umboni zinthu izi kwa inu, kuti zithandize mipingo. Ine ndine muzu ndi mbadwa ya Davide. Ndinenso nthanda yonyezimira.”

Cifukwa cha M’pingo wa Mulungu ndi oyera, Ambuye athu anatumiza kwa ife atumiki a Mulungu, ndipo Iye anawapanga kuchitira umboni zinthu zonse zimene zidzachitika. Wina amene anawapanga kuti achitire umboni zinthuzi ndi Yesu Khristu, Mulungu Iyeyekha amene wakhala M’pulumutsi wa oyera. 


Ndime ya 17: Mzimu ndi mkwatibwie akunenabe kuti: “Bwera!” Aliyense wakumva anene kuti: “Bwera!” Aliyense wakumva ludzu abwere. Aliyense amene akufuna, amwe madzi a moyo kwaulere. 

Ku aliyense mdzikoli lapansi amene akumva njala ndi ludzu la chilungamo cha Mulungu, Ambuye athu anawaitira ku Mawu a madzi a moyo. Aliyense amene akumva njala ndi ludzu la chilungamo cha Mulungu anapatsidwa dalitso lobwera kwa Ambuye, pokhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu wopatsidwa ndi Iye, ndipo ndiyeno pakumwa madzi a moyo. Ichi ndicho cifukwa chake Ambuye akulankhula ku wina aliyense kuti abwera kwa Yesu Khristu. Aliyense angalandire choonadi cha uthenga wa madzi ndi Mzimu mwaulere. Koma madzi a moyo ndiochotsedwa ku onse amene alibe funirolo. Ngati inu mfuna, inu, nanunso, mngamwe madzi a Moyo wopatsidwa ndi Ambuye pokhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu. 


Ndime ya 18: Ine ndikuchitira umboni kwa aliyense wakumva mawu a ulosi wa mumpukutuwu, kuti: Wina akawonjezera pa zimenezi, Mulungu adzamuwonjezera miliri yolembedwa mumpukutuwu; 

Malemba ndi Mawu a Mulungu. Choncho, ngati tikhulupilira mu Mawuwa, sitingaonjezere kapena kuchotsa ku iwo. Ndimeyi imatiuza kuti pakuti Mawu a Malemba ndi Mawu a Mulungu, kulibe wina aliyense angakhulupilire mu iwo poonjezera kapena kuchotsako kuchoka ku Mawu olembedwa a choonadi, kapena kukhulupilira potsiya kunja choonadi cholembedwa. Choncho tiyenera kukhala maso. Mawu aliwonse olankhulidwa ndi Mulungu ndi ofunikira; kulibe ena aliwonse amene angatsiyidwe ngati osafunikira. 

Komabe anthu apitirizabe kusula uthenga wa madzi ndi Mzimu wopatsidwa ndi Ambuye. Ichi ndicho cifukwa ngakhale tsopanoli sanaomboledwe kuchoka ku machimo awo. Cifukwa nciani iwo okhalabe ochimwa, ndipo cifukwa alowa mchionongeko chao—ngakhale kuti iwo akunena kuti okhulupilira mwa Yesu ngati M/pulumutsi wao. Kuti aombole ochimwa kuchoka ku uchimo, Ambuye athu anawapatsa madzi Ake ndi magazi (1 Yohane 5:4-5, Yohane 3:3-7). Komabe anthu ambiri akuika nzeru kwambiri mu magazi a Yesu oklha pa Mtanda; choncho, iwo akalibe kuomboledwa kuchoka ku machimo awo, choncho ndimmene adzakumanirana ndi miliri yonse yolembedwa mu Buku la Chivumbulutso. 

Onse amene akunena kuti okhulupilira mwa Yesu ndipo komabe akupitilizabe kusula choonadi kuti Khristu anachotsa machimo onse adziko lapansi mwa ubatizo Wake kuchokera kwa Yohane adzakumana ngakhalenso ndi chilango choopsya kwambiri cha gehena. Cifukwa nciani? Cifukwa iwo sakhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu umene Ambuye anawapatsa, ndipo choncho sanabadwe matsopano ngakhale tsopanoli. Wina aliyense amene akusula uthenga wa madzi ndi Mzimu woptsidwa ndi Ambuye adzalowa mnyanja yoyaka moto kwa muyaya ndipo adzakumana ndi kuzunzidwa—tsiku lopapatira lidzabweradi ku anthu otero. 


Ndime ya 19: Ndipo wina akachotsa kalikonse pa mawu a mumpukutu wa ulosi umenewu, Mulungu adzachotsa gawo lake pa zolembedwa mumpukutuwu, kutanthauza kuti sadzamulola kudya zipatso za m’mitengo ya moyo, ndipo sadzamulola kulowa mumzinda woyerawo. 

Kodi alipo pakati pathu wina aliyense amene chikhulupiliro chake chikutsiya Mawu achoonadi, akuti Yesu ananyamula machimo onse a anthu pa Iyeyekha polandira ubatizo kuchokera kwa Yohane M’batizi, ndi kuti kamodzi kokha Iye anachotsa machimo onse popachikidwa? Ngati n’tero, anthu otero adzatayadi ufulu olowa mu Mzinda Woyera wa Mulungu, cifukwa iwo sakhulupilira mu ubatizo umene Ambuye athu analandira kuchokera kwa Yohane kuti ananyamula machimo onse a anthu pa Iyeyekha mwa kamodzi kokha. Iwo pothera pake akuchita uchimo wa kusula uthenga wa madzi ndi Mzimu wopatsidwa ndi Ambuye. 

Choncho, Akhristu ayenera kusunga choonadi chakuti Yesu ananyala machimo a anthu mwa ubatizo Wake umene unalandira kwa Yohane mmitima yawo. Pokhapo achita tero, onse adzatsiyidwa ku ulemerero olowera mu Mzinda Woyera wopatsidwa ndi Ambuye. Ngati mkukhulupilira kuti Yesu ndi M’pulumutsi wanu, ndiyeno muyenera kusukidwa kuchoka ku machimo anu onse pokhulupilira ndi mtima wonse kuti Yesu anabwera padzikoli lapansi, anabatizidwa ndi Yohane mu Mtsinje wa Yordani kuti mwathunthu apulumutse anthu onse kuchoka ku machimo adziko lapansi, ndi kuti Iye kuchoka pamenepo anachotsa machimo onse anachitidwa ndi anthu powatenga tero pa Iyeyekha. Chinthu pa inu cimene chingasuke zonyansa zanu zonse ndi ubatizo umene Ambuye athu analandira. Atanyamula machimo athu adziko lapansi pa Iyeyekha, Ambuye anakhetsa mwazi Wake ndi kufa pa Mtanda kuti alipire mphoto ya machimo athu onse ndi imfa Yake. 

Ubatizo wa Yesu umene analandira kuchoka kwa Yohane M’batizi ndi chidzindikiro chotsimikizika cha chipulumutso chathu kuchoka ku uchimo. 1 Petulo 3:21 imatiuza, “Chofanana ndi chingalawacho chikupulumutsanso inuyo tsopano. Chimenechi ndicho ubatizo, (osati kuchotsa litsiro la m’thupi, koma kupempha chikumbumtima chabwino kwa Mulungu,) mwa kuukitsidwa kwa Yesu Khristu.” Tiyenera kudzindikira kuti Yesu ananyamula machimo onse adziko lapansi pa Mtanda anakhetsa mwazi Wake kotero kuti alipire mphoto ya machimo a anthu ndi imfa Yake, zonsezi mmalo mwathu. 

Ichi ndicho cifukwa Mulungu amapatsanso Mawu Ake ochenjeza anthu onse mndime ya 19. Tiyenera kukhulupilira mu Mawu a uthenga wa madzi ndi Mzimu mmene alili, kopanda kuonjezera kapena kuchotsako ku iwo. 


Ndime ya 20: Amene akuchitira umboni zinthu zimenezi akuti, ‘Inde, ndikubwera mofulumira.’ Ame! Bwerani, Ambuye Yesu! 

Ambuye anthu posachedwapa adzabweranso padzikoli lapansi. Ndipo oyera, amene analandira chikhululukiro cha machimo awo pokhulupilira mwa Ambuye amabvekedwa mu ulemerero wa Kumwamba, molimbika akuyembekeza kubwera kwa chiwiri kwa Ambuye. Pakuti onse amene okhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu onse ndi okonzeka kukumana ndi Ambuye akubwera ngakhale tsopanoli, akuyembekezera kuti Ambuye abwerenso ndi kuwabveka mu madalitso Ake olonjezedwa ku oyera. Choncho, oyera oyembekeza mofunitsitsa kubwera kwa chiwiri kwa Ambuye, mokhulupirika ndiponso moyamikira.


Ndime ya 21: Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu Khristu kukhale ndi oyerawo. Ameni. 

Mtumwi Yohane atsiliza Buku la Chivumbulutso ndi pemphero lopempha chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu kuti chikhale ndi onse amene ofuna kulowa mu Mzinda Woyera woptsidwa ndi Mulungu. Lekani, naifenso, tikhale oyera amene olowa mu Mzinda Woyera woptsidwa ndi Yesu Khristu kupitila muchikhulupiliro kosalephera.