Sermons

[22-2] < Chivumbulutso 22:1-21 > Khalani Osangalala ndipo Olimba mu Chiyembekezo cha Ulemerero< Chivumbulutso 22:1-21 > 


Chivumbulutso 22:6-21 imatiuza chiyembekezo cha Kumwamba. Chapitala 22, chapitala yotsilizitsa Buku la Chivumbulutso, ikulankhula za kutsimikiza kwa kudalirika kwa Malemba aulosi ndi kuitana kwa Mulungu kwa Yerusalemu wa Tsopano. Chapitalayi imatiuza kuti Yerusalemu wa Tsopano ndi mphatso ya Mulungu yopatsidwa ku oyera amene anabwadwa mwatsopano pokhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu. 

Mulungu anapanga oyera obadwa-mwatsopano kuyamika Iye Mnyumba ya Mulungu. cifukwa chaichi, Ine ndine aoyamikira kwambiri kwa Ambuye. Mawu sangaonetse mmene tilili othokoza pakutilora kukhala oyera amene, pokhulupilira mu tuehnga wa madzi ndi Mzimu, tinakhulukidwa ku machimo athu onse pamaso pa Ambuye. Kodi ndani padzikoli lapansi adzalandira dalitso lalikulu koposa limene tinalandira? Kulibe wina aliyense! 

Ndime yeniyeni ya tsiku lalelo ndi chapitala yomaliza ya Chivumbulutso. Mu Buku la Genesi, tikuona Mulungu kupanga ndodomeka ya anthu, ndipo mu Buku la Chivumbulutso, tikuona Ambuye athu akukwanilitsa zikonzero Zawo zonsezi. Mawu a Chivumbulutso angamasulidwe ngati chikonzero cha kuononga dzikoli kotero kuti akwanilitse nchito za Mulungu za anthu malinga ndi mmene Iye anakonzera. Kupitila mu Mawu a Chivumbulutso, tingaone Ufumu wa Kumwamba nthawi isanafike mmene unavumbulutsidwa ndi Mulungu. Maonekedwe a Mzinda wa Mulungu ndi Minda yake. 


Chapitala 21 ikulankhula za Mzinda wa Mulungu. ndime 17-21 ikutiuza: “Anayezanso mpanda wake, ndipo unali wautali mikono 144, malinga ndi muyezowa munthu, umene ulinso wofanana ndi muyezo wa mngelo. Mpandawo unali womangidwa ndi mwala wa yasipi, a ndipo mzindawo unaliwomangidwa ndi golidewoyenga bwino woonekera ngati galasi. Maziko a mpanda wa mzindawo anawakongoletsa ndi miyala yamtengo wapatali ya mitundu yonse: maziko oyamba anali amwala wa yasipi, achiwiri wa safiro, achitatu wa kalikedo, achinayi wa emarodi, achisanu wa sadonu, a 6 wa sadiyo, a 7 wa kulusolito, a 8 wa belulo, a 9 wa topazi, a 10 wa kulusopurazo, a 11 wa huwakinto, ndipo a 12, wa ametusito. Komanso zitseko za pazipata 12 zija zinali ngale 12. Chitseko chilichonse chinali ngale imodzi. Ndipo msewu waukulu wa mumzindawo unali wopangidwa ndi golide woyenga bwino woonekera ngati galasi.” 

Mawuwa a Chivumbulutso mafotokoza za Yerusalemu wa Tsopano umene Mulungu adzapereka ku anthu Ake obadwa-mwatsopano. Mzindawo wa Yerusalemu Kumwamba, timauzidwa kuti, unamangidwa ndi mitundu ya miyala 12 yotsiyanatsiyana ya mtengo wapatali, ndi zipata 12 zopangidwa ndi ngale. 

Ndiyeno Chapitala 22 ikulankhula za maonekedwe amene apezeka mu munda wa Mzinda wa Yerusalemu. Ndime ya 1 ikuti, “Ndipo anandionetsa mtsinje wa madzi a moyo, oyera ngati mwala wonyezimira wa kulusitalo, ukuyenda kuchokera kumpando wachifumu wa Mulungu, ndi wa Mwanawankhosa.” Mu Mzinda wa Mulungu, mtsinje wa kulusitalo akusefukira mu munda wake, monga mmene Mulungu anapangira mitsinje inayi kusefukira mu Munda wa Edeni pachiyambi. Mulungu amatiuza kuti uwu ndi munda umene olungama adzasangalala nawo kutsogolo. 

Ndime yeniyeni imene tawerenga imatiuzanso kuti mtengo wa moyo uli mkati mwa mundawo; kuti ikubala mitundu 12 ya zipatso, kubala zipatso zake mwezi uliwonse; ndi kuti masamba ake ndi ochiritsira mitundu ya anthu. Chikuoneka kwa ine kuti maonekedwe a Kumwamba ndi akuti sikuti ndi zipatso zake zokha zimadyedwa, komanso masamba ake, pakuti masamba ali n’mphavu yochiritsa. Madalitso Olandiridwa ndi Olungama! 


Baibulo limatiuza kuti mu Mzinda wa Mulungu, “Sikudzakhalanso temberero. Koma mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa udzakhala mumzindamo, ndipo akapolo a Mulungu adzachita utumiki wopatulikao kwa Iye. Iwo adzaona nkhope yake, ndipo dzina lake lidzakhala pamphumi pawo.” Imatiuza kuti ena aife amene anakhululukidwa machimo athu adzakhala kwa muyaya limodzi ndi Mulungu amene anatipulumutsa. 

Onse amene machimo awo anafafanizidwa pokhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu pamene anali padzikoli lapansi sadzalandira dalitso la machimo awo kuzimiririka lokha, komanso adzakhala ana a Mulungu, adzakhala ndi angelo ambiri kuwatumikira ngati iwo apaita mu Ufumu wa Kumwamba, ndi kukhala limodzi ndi Ambuye kwa muyaya. Ndime imatiuza kuti olungama adzalandira madalitso otero a osatha kuchokera kwa Mulungu ngati kuimilira pa mtsinje wa madzi a moyo ndi kudya zipatso za moyo, ndikuti ngati gawo limodzi la madalitsowo sikudzakhalanso matenda aliwonse. 

Imatiuzanso kuti iwo sadzafunanso kuwala kwa dzikoli kapena dzuwa, pakuti mu Ufumu olemekezeka wa Mulungu iwo adzakhala kwa muyaya limodzi ndi Mulungu, amene Iyeyekha ndi kuwala kwake. Ana a Mulungu amene analandira chikhululukiro cha machimo awo kupitila mu uthenga wa madzi ndi Mzimu, mmawu ena, adzakhala ngati Mulungu. ili ndi dalitso lolandiridwa ndi olungama. 

Mtumwi Yohane, mmodzi wa ophunzira a Yesu 12 amene analemba Buku la chivumbulutso, analembanso Uthenga wa Yohane ndi Mauthenga atatu a mu Pangano la Tsopano—Oyamba, Wachiwiri, ndi Yohane Wachitatu. Iye anaponyedwa mtendende pa Chilumba cha Patimosi cifukwa cha kukani kudzindikira mfumu ya Chiroma nagti mulungu. mkati mwa ndendeyi, Mulungu anatumiza mngelo Wake kwa Yohane ndi kumuonetsa zimene zidzachitika padzikoli lapansi, kuvumbuylutsa kwa iye chionongeka cha dziko ndi malo amene oyera pothera adzalowa ndi kukhala. 

Ngati tingamasulire Buku la Genesis ngati chikonzero cha chilengedwe, tingamasulire Buku la Chivumbulutso ngati kutsilizitsa kwa kung’ono kwa chikonzero. Kwa zaka 4,000, Ambuye athu anauza anthu kuti Iye adzapanga machimo awo onse kuzimiririka kupitila mwa Yesu Khristu. Ndipo mnthawi ya Pangano la Tsopano, pamene nthawi inabwera, Mulungu anakwanilitsa malonjezo Ake onse, akuti Iye adzatumiza yesu M’pulumutsi padzikoli lapansi, amene adzapanga machimo adziko lapansi kuzimiririka kupitila mu magazi a Khristu pa Mtanda. 

Pamene anthu anagwera mu chinyengo cha Mdyerekezi ndipo anagwidwa mu msampha wa chionongeko wake cifukwa cha uchimo, Ambuye athu Iye analonjeza kuti adzawaombola kuchoka ku machimo awo. Ndiyeno Iye anatumiza Yesu Khristu, Iye anamubatizidwitsa ndi kukhetsa magazi, kuchoka pamenepo anapulumutsa anthu mofikapo kuchoka ku machimo awo. 

Kupitila mu Mawu a Chivumbulutso, Mulungu analemba mozama mtundu wa ulemerero umene ukuyembekezo onse amene analandira chikhululukiro cha machimo awo, ndi chiweruzo cimene chiyembekezo ochimwa kumbali ina. Mulungu amatiuza, mmawu ena, kuli ambiri amene adzathera mgehena ngakhale kuti iwo akunena kuti okhulupilira mwa Iye mokhulupirika (Mateyu 7:21-23). 

Ambuye athu anapulumutsa ochimwa kuchoka ku machimo awo, ndipo Iye inatiuza kuti tisabitse Mawu a madalitso amene Iye anakonzera olungama. Kodi Ndani Osalungama ndi Wochita Zonyasa?


Ndime ya 11 ikuti, “Amene akuchita zosalungama, achitebe zosalungama, ndipo wochita zonyansa apitirizebe kuchita zonyansazo. Koma wolungama achitebe chilungamo, ndipo woyera apitirizebe kuyeretsedwa.” Kodi ndani “osalungama” apa? Osalungama ndi aja amene sakhulupilira mu chikondi cha uthenga wa madzi ndi Mzimu wopatsidwa ndi Ambuye. Pakuti anthu akuchita uchimo nthawi zonse, ayenera kukhupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu umene Ambuye anawapatsa ndipo kuchoka pamenepo kukhala moyo wao kumalemekeza Mulungu. Pakuti Mulungu ndi Yekhayo amene ayenerera kulandira ulemerero kuchokera ku anthu, ndipo cifukwa Iyeyekha ndi Amene anatibveka ndi chisomo Chake cha chipulumutso, tonse tiyenera kukhala moyo umene umapereka ulemerero kwa Mulungu. onse amene apandukira Mulungu ndi wochita zonyansa, cifukwa iwo sakhulupilira mu Mawu Ake tsiku ndi tsiku. 

Mu Mateyu 7:23, Ambuye athu anauza azipembezo amene anali kunena kuti okhulupilira mwa Iye ndi kumwa zawo, “Sindikukudziwani ngakhale pang’ono Chokani pamaso panga, anthu osamvera malamulo inu!” Ambuye athu anawatchula, “inu athu osamvera malamulo” Iye anawazunzura cifukwa anthuwa anali kukhulupilira mwa Yesu kupitila mu zochita zawo, mmalo mokhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu ndi mtima wonse. Kusamvera malamulo ndi tchimo, ndipo kusakhulupilira mu Mawu a Mulungu ndi mtima wa wina. Choncho, ngati anthu samvera malamulo pamaso pa Mulungu, chitanthauza kuti iwo sakhulupilira mchikondi ndi chipulumutso cha madzi ndi Mzimu cimene Mulungu anawaptsa iwo. Kusamvera malamulo n’kusintha Mawu a Mulungu kukhala mchifuniro iye mwene ndi kukhulupilira mnjira ina liyonse mmene wina angafunire. 

Onse amene okhulupiliradi mwa Yesu ayenera kumvomera zilizonse zimene Mulungu anakhazikisa mmene zilili. Tikukhulupilira mwa Yesu, koma mwazizizi ichi chimatilora kusintha chikonzero cha Mulungu ndi kukwanilitsa chipulumutso Chake. Uthenga wa mndime tawerenga ndi kuti Mulungu adzapereka moyo osatha ku onse amene okhulupilira mchipulumutso Chake monga mmene chikuimilira pa icho chokha, koma kutumiza mgehena onse amene akusintha Chilamulo cha Mulungu mnjira ina iliyonse imene ingawakomere. 

“Amene ndi osalungama, apitilizebe kukhala osalungama.” Ichi chimatiuza kuti anthu otero, mkuuma mtima wao, sakhulupilira mchikhulupilira monga mmene anakhazikitsira Mulungu. Iwo ndi osalungama. Ndipo ichi ndicho cifukwa nthawi zonse ochimwa ndi osalungama. 

Ndime ikupitilizabe, “ndipo wochita zonyasa, apitirizebe kuchita zonyasa.” Ichi chiimilira onse amene, ngakhale ndi ochimwa, ndipo ganizirani choona chakuti Yesu anapanga machimo awo kuzimiririka mwa madzi ndi Mzimu, saganizako za kuyeretsa machimo mwa chikhulupiliro. Motero, Mulungu adzawasiya okha anthuwa opanda chikhulupiliro mmene alili, ndipo ndiyeno kuwaweruza. Powapotsa anthu chikumbumtima, Mulungu anachipanga kukhala chotheka ku iwo kuti adzindikire uchimo mmitima yawo. Ndipo iwo ngakhale tsopanoli saganizirako kuyeretsa machimo awo mmitima yawo, ngakhale kudziwa uthenga wa madzi ndi Mzimu. Mulungu akutiuza kuti Iye adzawatsiya anthuwa mmene alili. 

Miyambo 30:12 ikuti, “Pali m’badwo umene umadziona kuti ndi woyera, koma sunasambe kuti uchotse ndowe zake.” Akristu-azipembezo a matsiku ano ndi anthu oti safuna ngakhale kusukidwa ku machimo awo. Koma, Yesu, amene ndi Mulungu Iyeyekha, anabwera padzikoli lapansi kuti apulumutse ochimwa, anachotsa machimo awo onse ponyamula machimo a anthu pa Iyeyekha mwa ubatizo Wake onse kwa nthawi imodzi, mwa kamodzi kokha anaweruzidwa cifukwa cha machimo onsewa mwa kupachikidwa, ndipo kuchoka pamenepo anapumulumutsadi ena aife amene tikukhulupilira kuchoka ku uchimo. 

Ku wina aliyense amene odziwa ndi kukhulupilira mu Mawu a uthenga wa madzi ndi Mzimu mwa umene Yesu Khristu anapulumutsira ochimwa, Ambuye athu analora munthuyu kuti akhululukidwe machimo ake onse, kosaganizira mtundu wa ochimwa mmene angakhalire. Ndipo koma ngakhale tero akalikobe anthu amene sanalandire chikhululukiro cimemechi cha uchimo kupitila mchikhulupiliro. Awa ndi amene anaganiza iwo okha kusayetsa ngakhalenso machimo awo kuti achotsedwe. Mulungu adzawalora kukhala mmene alili. 

Uku ndi kukwanilitsa chilungamo cha Mulungu. Ndikuonetsa kuti Mulungu ndi Mulungu wa chilungamo. Anthuwa adzaponyedwa mmoto wa sulufule umene ukuyaka kwa muyaya. Ndiyeno iwo n’pamene adzazindikira amenedi ndi Mulungu wa chilungamo. Ngakhale kuti akumvomera kuti Yesu ndi M’pulumutsi wao, iwo sakunyenga kokha chikumbumtima chawo, komanso akudetsa chikumbumtima cha ena. Cifukwa iwo anakana uthenga wa madzi ndi Mzimu, Muolungu, adzabwezera malinga ndi zimene anachita. Ngati tsiku labwera, Mulungu adzabweretsa mkwiyo Wake ku onse amene ayenerera mkwiyo Wake. Pereka ku Wina Aliyense Malinga ndi Nchito Yake


Kuli mitundu iwiri ya anthu padzikoli lapansi: ena anakumana ndi Ambuye, ndipo ena sanakumane naye. Ambuye athu adzabwezera ku wina aliyense malinga ndi nchito yake. 

Kulibe wina aliyense amene angayeretsedwe pa iye yekha, koma kuyeretsedwa kumachokera kwa Yesu. Iye ananyamula machimo onse a anthu pa Iyeyekha mwa ubatizo Wake mwa kamodzi kokha, ananyamula machimo adziko lapansi pa Mtanda, ndipo pa Mtanda anakumana ndi chiweruzo chonse cha uchimo cimene anthu adzakumana nacho. Anthu ayenera kukhala olungama pokhulupilira mchoonadichi. Onse amene okhulupilira mchoonadichi ndi amene anakumana ndi Ambuye. 

Mulungu apempha onse amene alibe uchimo, amene odziwa ndi kukhulupilira mchoonadichi, kuti alalike uthenga mdzikoli lapansi ndi kusunga Mawu Ake woyera monga mmene okhalabe moyo. Mulungu akunena kuti, “iye amene ndi olungama, apitirizebe kukhala olungama.” Tiyenera kusunga lamuloli mmitima yathu, kuti titeteze chikhulupiliro chathu choyera, ndi kulalika uthenga wokoma tsiku ndi tsiku. Cifukwa nciani? cifukwa anthu ambiri mdzikoli lapansi okhalabe osadziwa za uthengau oona, ndipo monga zotulukamo chikhulupiliro chao chonse ndi cholakwika. 

Kuli amene amakhalira kumbuyo mofikapo chiphunzitso cha kuziyeretsedwa padzikoli lapansi. Ngakhale kuti Ambuye athu anapanga kale machimo a anthu kuzimiririka, anthuwa amapemphera za chikhululukiro cha machimo awo tsiku ndi tsiku ngakhale tsopanoli. Kupereka mapemphero akulapa tsiku ndi tsiku, akuyetsa kuchotsa machimo awo, kuti aziyeretse kotero kuti mpaka akhale olungama amene sadzachitanso uchimo uliwonse, ndipo kutero kuti afanane ndi Yesu. Koma Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, ndi Mfumu, Mneneri ndiponso Wansembe Wamkulu. 

Mtumiki oona wa Mulungu sagwira chabe nchito yakuonetsetsa kuti wina aliyense akhululukidwadi uchimo, koma iwo amatsogoleranso aliyense ku choonadi ngati ogwira nchito-pamodzi a Mulungu. Atumiki a Mulungu ndi amene, kupitila mu Mawu olembedwa, ali ndi kudziwa kweni kweni kwa zinthu zimene zidzachitika. 

Ndime ya 12-13 ikuti, “Taonani! Ndikubwera mofulumira, ndipo mphoto ndili nayo, yoti ndipereke kwa aliyense malinga ndi ntchito yake. Ine ndine Alefa ndi Omega, woyamba ndi wotsiriza, chiyambi ndi mapeto.”

Ambuye athu ndi Alephadi ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza, Chiyambi ndi Mapeto. Tiyenera kukhulupira mu zinthu zilizonse zimene Ambuye analankhula kwa ife mwa mantha. 

Ambuye anthu adzadalitsa oyera ndi madalitso amene ndi aakulu kwambiri koposa nchito zawo, pakuti Iye ndi olemekezeka ndiponso wachifundo. Iye ndi wachifundo ndiponso okoma mtima Wina amene anatipulumutsa kuchoka ku Machimo athu onse, ndipo, monga mmene Mawu a Chivumbulutso amatiuzira, Mulungu wamphamvu ndi olungama amene adzakwanilitsa nchito Yake ya chipulumutso. Ndipo kukwanilitsaku kwa chipulumutso, kumene kuli pafupi kubwera, kumalora ku oyera chipata cholemekeza cha mu Mzinda wa Yerusalemu, mphoto za okoma mtima ndiponso zokwanira bwino za Ambuye athu za nchito zawo. Odala ndiwo Amene Amachita Malamulo Ake


Kupitiriza ndi ndime ya 14, ndime yeni yeni imatiuza kuti, “Odala ndiwo amene achapa mikanjo yawo, kuti akhale ndi ufulu wa kudya zipatso za m’mitengo ya moyo, ndiponso kuti akalowe mumzindawo kudzera pazipata zake.” Kuli anthu ambiri amene akunena, kuimilira pa ndimeyi, kuti chipulumutso chimabwera mwa nchito—poonetsetsa, mmawu ena, malumulo Ake. 

Koma choona, “Kuchita malamulo Ake” chitanthauza kukhulupilira ndi kusunga Mawu onse olembedwa a Mulungu mwa chikhulupiliro. Yohane Mtumwi analemba kuti, “Lamulo lake ndi lakuti, tikhale ndi chikhulupiriro m’dzina la Mwana wake Yesu Khristu ndiponso tizikondana, monga mmene iye anatilamulira” (1 Yohane 3:23). Choncho, ngati takhulupilira mu uthenga oona wa madzi ndi Mzimu, ndi kuzipereka ife tokha pa kulalikira uthenga kuti tipulumutse miyoyo yonse yosochera mdziko lonse lapansi, tikuchita malamulo Ake pamaso pa Iye. 

Choonadi ndi chakuti machimo onse amene tikuchita miyoyo yathu yonse anafafanizidwa kale kupitila mu ubatizo umene Yesu analandira kwa Yohane M’batizi. Kusatira pa ubatizou, magazi a Ambuye athu pa Mtanda, kuukitsidwa Kwake, ndi kukwera Kwake kwatipanga ife kubadwa mwatsopano ndi kutilora kukhala moyo watsopano muchoonadi Chake. 

Paliponse ngati tagwera mu uchimo titabwa kale mwatsopano, tiyenera kubwereranso ku Mawu a choonadi amene anatisuka ku machimo athu onse; kudzindikira kuti njira zathu zili ngati sitingaleke koma kuchimwa; ndiponso, n’kubwereranso ku chikhulupiliro cha mu Mtsinje wa Yordani mmene Ambuye athu ananyamula kufooka kwathu, kuperewera, ndi machimo, batizidwani limodzi ndi ubatizo wa Yesu ndipo ikidwani limodzi ndi Khristu amene anafera pa Mtanda. Ngati tachita tero, mpaka tingamasuke kuchoka ku machismo amene tachita titabadwa kale mwatsopano, ndi kusukidwa. Kugwilirira ku chilungamo cha Mulungu poimanso njii mu chipulumutso chathu chosatha cha kukhululukidwa ndi kumuthokoza Iye cifukwa cha chipulumutso Chake changwiro ndiponso chosatha. 

Yesu anachotsa kale machimo adziko lapansi. Bvuto limapezeka ndi chikumbumtima chathu. Ngakhale kuti Ambuye athu anasamalira kale machimo adziko lapansi mwa ubatizo Wake, cifukwa ife anthu sikudzindikira kuti chotero Ambuye athu anachotsa machimo athu mwa ubatizo ndi kupachikidwa Kwake, chikumbumtima chathu chikukhalilira chobvutidwa ngati ochimwa. Choncho ife ndife oyenerera kumva kuti tikalibe ndi uchimo otsala mwa ife, pamene mchoona cimene tiyenera kuchita ndi kumangokhulupilira kuti machimo athu onse anachotsedwa kale kupitila mu uthenga wa madzi ndi Mzimu wopatsidwa ndi Yesu Khristu. 

Ngati mtima yathu yakhumudwa ndi machimo athu, kodi ndi choonadi chotani cimene tingachiritsire zilonda za machimowa? 

Zilondazi, nazonso, zonse zingachiritsidwe pokhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu—umene ndi, pokhulupilira kuti Ambuye ananyamula machimo onse adziko lapansi pa Iyeyekha pobatizidwa ndi Yohane mu Mtsinje wa Yordani, ndi kuti Iye anapanga onse machimowa kuzimiririka powanyamulira pa Mtanda wa Kavali ndi kukhetsa mwazi Wake paumenewo. Mmawu ena, machimo azochita zathu amene tikuchita titalandira chikhululukiro cha uchimo nazonso zingachotsedwe ngati tasimikizanso chikhulupiliro chathu mu uthenga kuti Yesu Khristu anachotsa kale machimo athu onse, kuphatikizapo machimowa a zochita zathu. 

Machimo adzikoli anachotsedwa mwa kamodzi kokha pamene Yesu Khristu analandira ubatizo Wake ndipo Iye anapachikidwa. Choncho, ngakhale machimo adziko lapansi kapena machimo a munthu a zofuna zathu kuti okhale osukidwa kuwiri kapena katatu, ngati ndi pamene iwo ayenera kusukidwa kopitiriza. Ngati wina aphunzitsa kuti chikhululukiro cha uchimo chimakwanilitsidwa pang’ono pang’ono, ndiyeno uthenga umene iye akulalikira ndi uthenga wachinyengo. 

Mulungu anapanga machimo adziko lapansi kuzimiririka mwa kamodzi kokha. Ahebri 9:27 imatiuza kuti, “Monga mmene zilili ndi anthu kuti amayembekezera kufa kamodzi kokha, kenako n’kudzalandira chiweruzo.” Monga mmene tikufa kamodzi kokha cifukwa uchimo, ndi chifuniro cha Mulungu kuti tilandirenso chikhululukiro cha uchimo kamodzi kokha. Kubwera padzikoli, Yesu Khristu ananyamula machimo athu onse pa Iyeyekha kamodzi kokha, anafa kamodzi kokha, ndipo anaweruzidwa mmalo mwa ife kamodzi kokha. Iye sanachite zinthuzi kwa nthawi zambiri.

Ngati talandira chikhululukiro cha uchimo pokhulupilira mwa Yesu Khristu ndi mitima yathu, ndiyeno, ndi choyenera kuti ife tikhulupilire kamodzi kokha ndi kulandira chikhululukiro chosatha cha machimo athu onse. Cifukwa machimo amene tikuchita kuchoka pamenepo amapweteka mitima yathu nthawi ndi thawi, cimene tiyenera kuchita ndi kupita pamaso pa Mawu a chipulumutsochi, chakuti Ambuye athu anachotsa machimo athu onse kamodzi kokha, ndi kusukidwa ndiponso kuchiritsidwa mitima yathu yonongeka mwa chikhulupiliro: “Ambuye, Ndine odzaza ndi zonyansa. Ndachitanso uchimo. Ndalephera kukhala moyo wonse malinga ndi chifuniro Chanu. Koma pamene Inu munabatizidwa ndi Yohane mu Mtsinje wa Yordani ndi kukhetsa mwazi pa Mtanda, kodi Inu simunasamale machimo angawa naonso? Haleluya! Ndikuthozani Inu, Ambuye!” 

Ndi chikhulupiliro chotero, tingatsimikizirenso chikhululukiro chathu cha uchimo ndi kuthokoza Ambuye tsiku ndi tsiku. Chapitalayi yomaliza ya Chivumbulutso imatiuza kuti mwa kupita pamaso pa Yesu Khristu, amene ndi mtengo wa moyo, ndipo pokhulupilira kuti Ambuye anasuka kale machimo onse adziko lapansi, onse amene analandira chikhululukiro cha uchimo anapeza ufulu wa kulowera mu Ufumu wa Mulungu, Mzinda Woyera, kupitila mchikhulupiliro.

Aliyense amene afuna kulowa mu mzinda wa Mulungu ayenera kukhulupilira kuti Yesu Khristu anapepetsa machimo a anthu kwa muyaya polandira ubatizo Wake kamodzi kokha ndi kukhetsa mwazi Wake. Ngakhale tinali ndi zochita za zonyansa, pokhulupilira mu ubatizo ndi mu mwazi wa Yesu Khristu M’pulumutsi wathu, chikhulupiliro chathu chingathokozedwe ndi Mulungu ngati choona, ndipo tonse tigapite pamaso pa mtengo wa moyo. 

Kungokhulupilira mu ubatizo wa Khristu ndi mwazi kokha kodi tingakhale ndi ufulu wa kumwa madzi a moyo amene akuyenda yenda mu mzinda wa Yerusalemu wa Tsopano ndi wa kuzipatso za mtengo wa moyo. Cifukwa cofunikira cha kulowera Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi, cimene singaloredwe kuchotsedwa ndi wina aliyense, chimachokera ku uthenga wa madzi ndi Mzimu okha, tiyenera kuteteza chikhulupilira chathu ndi kuchilakiranso ku ena. Chimodzi-modzi, mawu akuti “(ku) chita malamulo Ake” atanthauza kuti ife tipambane dziko lapansi mwa chikhulupiliro—cimene ndi, kukhulupilira mu ndi kusunga uthenga wa madzi ndi Mzimu, ndiponso kuzipereka tokha polalikira uthenga oona mdziko lonse lapansi. 

Mu Mateyu 22, Yesu amatiuza “mwambi wa chikondwelero cha ukwati.” Kumasulira kwa mwambiu ndi kuti onse amene alibe chobvala chawo cha ukwati ayenera kuponyedwa mu mdima (Mateyu 22:11-13). Kodi tingabvale bwanji chobvala cha ukwati chathu kuti titengeko mbali mmgonero wa ukwati wa Mwanawankhosa, ndipo kodi zobvala za ukwati n’zotani? Zobvala za ukwati zimene zimatilora kulowa mmgonero wa ukwati wa Mwanawankhosa ndi chilungamo cha Mulungu chopatsidwa kwa ife kupitila mu uthenga wa madzi ndi Mzimu. Kodi mkukhulipilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu? Ngati n’tero, ndiyeno ndi obvekedwa mokongoletsedwa kwambiri mchilungamo Chake kotero kuti mngalowe Kumwamba ngati mkwatibwi opanda uchimo wa Mwana. 

Ife, obadwa—mwatsopano, nasenso timachita uchimo tsiku ndi tsiku. Choncho, ndi olungama okha amene anakhululukidwa machimo pamaso pa Mulungu ndiwo amene ayenerera kusuka machimo awo a tsiku ndi tsiku kuchoka ku zobvala zawo za chilungamo mwa chikhulupiliro. Cifukwa onse amene machimo awo sanakhululukidwe sayenerera kusuka machimo awo, sadzakwanitsa pa iwo okha kusuka machimo awo ndi mapemphero awo a kulapa a tsiku ndi tsiku. Kuti tinapulumutsidwa kuchoka ku machimo adziko lapansi pokhulupilira mwa Ambuye zonse zinakhala zotheka podziwa ndi kukhulupilira kuti Ambuye anachotsa machimo athu onse adziko lapansi pobwera padzikoli lapansi, kubatizidwa, ndi kukhetsa mwazi Wake. 

Timatsimikiza, mmawu ena, kuti machimo athu a tsiku ndi tsiku anachotsedwa kale mu uthenga Wake okha oona. Onse amene analandira chikhululukiro cha uchimo kuchokera kwa Ambuye kupitila mu Mawu a madzi ndi magazi angakuzidwenso za chipulumutso chawo kuchoka ku machimo amene iwo akuchita pamene ali kukhala ndi miyoyo yawo. 

Ndi cifukwa Ambuye athu anapanga machimo athu kuzimiririka onse kamodzi kokha kotero kuti ife tingasuka machimo amene tikuchita ndi zochita zathu pokhulupilira mchipulumutsochi cha kupepetsa kwa muyaya. Kuti ichi chinalibekathu, kuti Ambuye sanasuke machimo athu onse kamodzi kokha, mmawu ena, kodi ife tikanakhala bwanji opanda uchimo?

Kodi tingalowe motani mu Mzinda Woyera wa Kumwamba? Kodi tingapite motani pamaso pa Yesu Khristu, mtengo wa moyo? Pokhulupilira mwa Ambuye athu amene anapanga machimo athu onse kuzimiririka, tingalowe mu Ufumu wa kumwamba ngati anthu oyera ndiponso opanda chilema; ndipo ngati paliponse tikuchimwa mu miyoyo yathu, popita pamaso pa Ambuye ndi kutsimikiza kuti Iye apanganso machiwowa kuzimiririka, tingamasulidwe kuchoka ku machimo otero. N’cifukwa chake Ine ndikukuuzani kuti ndi okhawo obadwa—mwatsopano ali ndi mpata okhululukidwa machimo awo a tsiku ndi tsiku mwa chikhulupiliro. 

Mfumu Davide anachita machimo aakulu pamaso pa Mulungu, ngakhale iye anali mtumiki wa Mulungu. Iye anachita dama ndi mkazi okwatiwa, ndipo anapha mwamuna wake amene anali ogonera wake. Komabe, iye anayamika Mulungu cifukwa cha chikululuko Chake chokomera mtima motere: 

“Wodala ndimunthu amene wakhululukidwa zolakwa zake, amene machimo ake aphimbidwa.

Wodala ndimunthu amene Yehova sanamusungire cholakwa chake,

Amene alibe mtima wachinyengo (Masalimo 32:1-2).”

Kodi ndani amene ndi wodala kwambiri mdzikoli lapansi pamaso pa Mulungu? Wodala ndi aja aife amene anabadwa mwatsopano; amene anapulumutsidwa; ndiponso amene, paliponse pamene uchimo wachitidwa mu miyoyo yathu, timayapenya pa choona chakuti Ambuye anapanga machimo athu onse kuzimiririka, kupita kukasupe wa moyo tsiku ndi tsiku, ndi kusuka mitima yathu yothimbira tsiku ndi tsiku. Uku ndikulangalira pa kuomboledwa kwathu ndi kutsimikizira chisomo za Ambuye athu chachikulu cha chipulumutso. 

Olungama ndiwo amene analandira chikhululukiro cha uchimo, kupanga zolakwa zawo zonse kuchiritsidwa, zochita zawo kuchiritsidwa, ndiponso chimodzimodzi mitima yawo. Choncho titakhala olungama opanda chilema, ndiyeno tingalowe mu Ufumu wa Kumwamba. Ngati tingamvomere chabe zimene Yesu Khristu, chipata chachipulumutso ndiponso mtengo wa moyo, anatichitira ife, mphamvu Yake ingavumbulutsidwe, ndipo ife choncho tingalandire chikhululukiro cha uchimo ndi kulowa Kumwamba. Onse Amene Akupita Pamaso pa Mtengo wa Moyo


Cifukwa cimene ena aife amene tinalandira chikhululukiro cha uchimo tsiku ndi tsiku tikupita pamaso pa Ambuye ndi kutsimikiza kuti Ambuye athu anapanga machimo athu onse kuzimiririka, kuti tilangalilenso pa chisomo chachipulumutso, kuti tichikumbuke, ndi kuyamika Mulungu cha icho, kotero kuti tonse tikhala okwanilitsa koposa kuti tilowe mu Ufumu Wake. Ichi ndicho cifukwa chake tikulalikira uthenga. 

Nambala yosawerengeka ya Akristu, imalephera kukumana ndi atumiki a Mulungu amene angawatsogolere powaphunzitsa Baibulo moyenerera, ndiwopelewera pakusamvetsetsa kwao kwa Mawu ndi zikhulupiliro zawo zolakwika. Ngakhale tsopanoli, kuli anthu amene adzaza ndi zochita zawo, kupeleka mapemphero akulapa mmamawa mulimose ndi utsiku wonse. Cifukwa iwo akuchita zinthu zonsezi? Cifukwa iwo akukhulupilira kuti pakuchita tero, machimo awo angakhululukidwe. Ndipo iwo akukhulupilira tero cifukwa anaphunzitsidwa chiphunzitso cholakwika. Koma izi ndi nchito lokwika pamaso pa Mulungu. Anthu otero ndi achisoni kwambiri amene sakudziwa ngakhale chilungamo cha Mulungu kapena chikondi Chake chosakondera. 

Baibulo si chinthu cimene chingatengedwe mopepuka, ngati ndi kuti ingamasulidwe mnjira ina iliyonse mmene wina afunira. Ndipo komabe cifukwa anthu aimasulira, aphunzitsa, ndipo anakhulupilira mu iyo kuimilira pa mu maganizo awo opanga—munthu, zotuluka zakhala ngati pamwambapo—cimene ndi kuti, iwo akhalabe osadziwa chilungamo cha Mulungu ndi chikondi. Ndime iliyonse ya Baibulo ili ndi tanthauzo lake lenileni, ndipo ingamasulidwe moyenera ndi aneneri a Mulungu amene analandira chikhululukiro cha machimo. 

Kupita pamaso pa mtengo wa moyo ndi kwa ife kuti tikhulupilire mwa Ambuye pamene tikali padzikoli lapansi, kuti tizikumbukira tsiku ndi tsiku kuti Ambuye athu anapanga machimo onse kuzimiririka, kuti timuyamike Iye, ndi kuti tilalikire uthengawu. Ife, obadwa-mwatsopano, ndi kutinso tikumbukire kuti Iye ananyamula machimo pa Iyeyekha, kuti tisimikizire choonadichi tsiku ndi tsiku, kumupembeza Iye ndi chisangalalo cha kuyamikira, ndi kupita pamaso pa Ambuye athu. 

Ngakhale choncho, si chinthu choganiziridwa chabe kulankhula kuti Akristu mdziko lonse lapansi anamasulira molakwika ndimeyi ndi kukhulupilira molakwika kuti iwo angalowe mu Ufumu wa Mulungu posuka machimo awo kwa tsiku ndi tsiku kupitila mu mapemphero akulapa. Koma ichi si cimene ndime ikutanthauza. 

Pambuyo polandira chikhululukiro cha uchimo. Mitima yathu ingakhalebe mu ufulu potsimikizira kuti Ambuye athu anapanga machimo athu onse amene tikuchita ndi zochita zathu kuzimiririka. Potsimikizira chikhululukiro cha uchimo wathu ONSE, si ndife omangidwanso ndi uchimo. Iyi ndi njira yopitira pamaso pa mtengo wa moyo Kumwamba. 

Malembo ali mmuyetso otsiyaniranatu ndi maganizo-opanga munthu. Choncho, kuti tidziwe choonadi, poyamba tiyenera kuphunzira ndi kumvetsera choonadi kuchokera ku atumiki a Mulungu obadwa-mwatsopano. Onse Amene Ali Kunja Kwa Mzinda


Ndime ya 15 ikuti, “Kunja kuli anthu amene ali ngati agalu, amene amachita zamizimu, adama, opha anthu, opembedza mafano, ndi aliyense wokonda kulankhula ndi kuchita zachinyengo.” Mawu oimilira onse a nthawi zomaliza amene si obadwa mwatsopano. Ndichodabwitsa kuti Ambuye athu adzayetsa anthu otero ndi choonadi chotero. 

Khalidwe limodzi la agalu ndi kuti amabwereza—kumene ndi, amaluka zimene adya, n’kudyanso, ndipo ndiyeno n’kulukanso, ndipo ndiyeno n’kudyanso zimene alukazo. Ambuye athu apa akuti awa ndi “agalu” sadzakwanitsa kulowa mu Mzinda. 

Kodi ndiyeno agaluwa akuimilira ndani? Kuli anthu amene akufuura, “Ambuye, Ndine ochimwa; chonde chotsani machimo anga,” ndipo ndiyeno kumayamika Mulungu kuyimba, “Ndakhululukidwa, mwakhululukidwa, tonse takhululukidwa!” Koma kanthawi kosatilapo, anthuwa kamodzinso akufuula, “Ambuye, Ndine ochimwa, ngati Inu mngandikhululukirenso kwa nthawi iyinso, si Ndizachimwanso.” Iwo ndiyeno akuimbanso, “Ndakhululukidwa ndi Magazi a pa Khalavari!”

Anthuwa amabwereranso ndi kubwereranso kwambiri kotero kuti palibe wina amene atsimikizira kuti mwina anakhululukidwadi kapena ai. Anthu a mtundu otero ndi “agalu” amene Baibulo akulankhulapo. Agalu akuwuwa tsiku ndi tsiku. Akuwuwa mmamawa, akuwuwa mmazulo, akuwuwa mmbandakucha. Anthuwa sakuwuwadi mnjirayi, koma akufuula kuti iwo ndi ochimwa, ngakhale kuti iwo anakhululukidwa machimo awo. Akukhala olungama mu mphindi imodzi, akukhalanso ochimwa mumphindi yosatirapo.

Mnjirayi, ali ngati agalu zimene zimaluka zimene zilimkati ndi kudyanso, ndipo ndiyeno kulakanso kotero kuti zidyenso nthawi ina. Mofupikitsa, Baibulo amalankhula za Akristu amene okhalabe ndi uchimo mmitima yawo ngati “agalu.” Agalu sangalowa Kumwamba, koma ayenerera kukhala kunja kwa Mzinda. 

Chisatilapo, kodi amene ndi “ochita za mizimu ndani?” Awa ndiwo amene, amatengerapo mpata pa zokumba za opita kuchalichi-opanda kalema, amawabela ndalama zawo ndi zolankhula zawo-zachinyengo, ndi amene akusocheretsa anthu ndi zizindikiro za boza ndiponso zodabwitsa kunena kuti akuchiritsa matenda awo. Cifukwa onse akutenga dzina la Mulungu pachabe, sangalowa mu Mzinda Woyera. 

Ndiponso, ochita dama, opha anthu, opembeza mafano, ndi wina aliyense amene okonda ndi kunena boza sangalowa mu Mzinda. Ngati nthawi yomaliza yabwera, agalu ndi ochita zamizimu adzasocheretsa anthu, ndipo Wosusa Khristu adzaonekera. Wosusa Khristu amene amasocheretsa anthu Ambiri zodabwitsa zaboza ndi zizindikiro, akuba miyoyo yawo, akususana ndi Mulungu, ndipo afuna kuzikweza pamwamba iyeyekha koposa Mulungu ndi kupembezedwa, ndipo omusatira ake onse sadzakwanitsa kulowa mu Mzinda. 

Choncho, ngati tagwera muchinyengo cha onse amene akunena kuti tikukhalabe ndi uchimo, kapena tagwera mchinyengo cha zizindikiro ndi zodabwitsa zimene zikunyamutsa zokumba zathu, tonse tidzatsilizira kunja kwa Mzinda limodzi ndi Wosusa Khristu ndi Satana, kulira kofuula ndi kusheta mano, monga mmene Mawu amatichenjezera. 

Ndime ya 16-17 ikuti, “‘Ine, Yesu, ndinatumiza mngelo wanga kudzachitira umboni zinthu izi kwa inu, kuti zithandize mipingo. Ine ndine muzu ndi mbadwa ya Davide. Ndinenso nthanda yonyezimira.’ Mzimu ndi mkwatibwie akunenabe kuti: “Bwera!” Aliyense wakumva anene kuti: “Bwera!” Aliyense wakumva ludzu abwere. Aliyense amene akufuna, amwe madzi a moyo kwaulere.” 

Kodi munalandira chikhululukiro chanu cha uchimo kwaulere? Kupitila mu Mzimu Woyera ndi mu M’pingo wa Mulungu, Ambuye athu anatipatsa uthenga wa madzi ndi Mzimu umene umatilora kuti timwe madzi a moyo. Aliyense amene akumva njala ya chilungamo cha Mulungu, aliyense amene akumva ludzu la Mawu achoonadi, ndiponso aliyense afunitsitsa kulandira chikhululukiro cha uchimo—ku onse anthu otero, Mulungu anapereka kuwabvalika mu chifundo Chake ndipo anaikilako kuitana Kwake mpaka mu Mawu Ake, madzi a moyo a chipulumutso Chake. Kulandira chikhululukiro cha uchimo ndi njira yokhayo yoyankhira ku kuitanidwaku kwa Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi kumene madzi a moyo akuyenda yenda. Ameni, Bwerani Ambuye Yesu! 


Ndime ya 19 ikuti, “Ndipo wina akachotsa kalikonse pa mawu a mumpukutu wa ulosi umenewu, Mulungu adzachotsa gawo lake pa zolembedwa mumpukutuwu, kutanthauza kuti sadzamulola kudya zipatso za m’mitengo ya moyo, ndipo sadzamulola kulowa mumzinda woyerawo.” Pamsao pa Mulungu, sitingakhulupilire mnjira ina iliyonse imene tifuna kuimilira pa maganizo athuathu. Ngati n’cholembedwa mu Mawu a Mulungu, zimene ife tinganena ndi “inde,” pakuti ngati wina aliyense akananena kuti “ai” ku Mawu, Ambuye athu naonso angamutaire kutali, polankhula kuti, “Iwe si ndiwe mwana Wanga.” Ichi ndicho cifukwa chake tiyenera kukhulupilira mwa Iye malingano ndi Mawu. Si tingaonjezere kupena kuchotsera ku Mawu aliwonse a Mulungu, koma tiyenera kukhulupilira mu iwo mmene analembedwera. 

Kugwililira ku atumiki a Mulungu ndi kukhulupilira mu zimene Mzimu Woyera akulankhula kupitila mu M’pingo wa Mulungu ndi zimenezo za chikhulupiliro choona. Komabe anthu ambiri, monga mmene iwo anachotsera uthenga wa madzi ndi Mzimu kuchoka ku chikhulupiliro chao, okhalabe ndi uchimo mmitima yawo. Ngakhalenso pamene Mawu mobwereza amawauza kuti ndi okhawo amene alibe uchimo angalowe mu Mzinda Woyera wa Mulungu, iwo akutsiyabe ubatizo wa Yesu kuchoka ku chikhulupiliro chao, ndipo mmalo mwake oonjera ku icho mkunena kwao kotero kwa zochita ngati zopereka mapemphero akulapa ndi zopereka za zinthu za kutundu. 

Onse amene okhulupilira mwa Yesu ngati M’pulumutsi wao ayenera kukwanitsa kumvomera mwa chikhulupiliro chao kuti machimo onse a anthu anaikidwa pa Yesu kupitila mu ubatizo umene Yesu analandira kuchokera kwa Yohane M’batizi mu Mtsinje wa Yordani. Ngati mkuchotsako ubatizo wa Yesu mchoona mkutsiya chikhulupiliro chanu. Mmawu ena, ngati si mkhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu, ngakhale mwazi wa pa Mtanda ulibe tanthauzo, ndi chiukitso cha Khristu, nachonso, n’chosafunikira kwa inu. Ndi okhawo amene okhulupilira kuti Mulungu anapanga machimo awo kuzimiririka mwaulere ndi ofunikira ku chiukitso cha Yesu, ndipo ndi okhawa amene angafuule mkweza pobwera kwa Ambuye Yesu, monga mmene Mtumwi Yohane anachitira mndime ya 20. 

Ndime ya 20 ikuti, “Amene akuchitira umboni zinthu zimenezi akuti, ‘Inde, ndikubwera mofulumira.’ “Ame! Bwerani, Ambuye Yesu!” Ndi olungama okha amene angalanene ichi. Ambuye athu posachedwa adzabwera padzikoli lapansi, malinga ndi mapemphero a olungama. Ndi olungama okha, amene analandira chikhululukiro cha uchimo pokhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu, adzasangalala ndi kuyembekeza mofunitsitsa pobwera mofulumira kwa Ambuye. Ichi n’cifukwa chakuti onse amene ndi okonzeka kulandira Ambuye ndi okhawo amene anabvekedwa chobvala cha uthenga wa madzi ndi Mzimu—amene ndi, onse amene alibe uchimo. 

Ambuye akuyembekeza tsiku pamene Iye adzayankhira kuyembekeza kwa olungama, tsiku pamene Iye abwerera padzikoli lapansi. Iye adzatipatsa mphoto ya Ufumu wa zaka Chikwi chimodzi, ndi kutibveka ife, amene ndi olungama, mu madalitso Ake aakulu a kulowera Kumwamba kwa Tsopanoa ndi Dziko lapansi kumene madzi a moyo akuyendayenda. Kuyembekezaku kwa Ambuye sikuli kutali kwambiri. Choncho, zimene tingachite ndi kunena chabe, “Ameni. Ngakhale tero, bwerani, Ambuye Yesu!” ndipo n’chikhulupiliro ndi matamando, molimbika tikufunitsitsa kubweranso kwa Ambuye. 

Pomaliza, ndime ya 21 ikuti, “Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu Khristu kukhale ndi oyerawo. Ameni.” Mtumwi Yohane anatsiriza Buku la Chivumbulutso ndi pemphero lake lothera la madalitso ku wina aliyense. Iye anapereka pemphero lake la dalitso pomaliza, ndi mtima wake kuyembekezera kuti wina aliyense akhulupilire mwa Yesu, pulumutsidwani, ndipo lowani mu mzinda wa Mulungu. 

Okondedwa anga oyera, kuti tinapulumutsidwa ndi Mulungu chitanthauza kuti Iye anatikonda, anatiombolo kuchoka ku machimo athu onse, ndi kutipanga anthu Ake. Choncho ndichabwino ndiponso chothokoza kuti Mulungu anatipanga kukhala olungama kotero kuti tilowe mu Ufumu Wake. 

Apa ndi penipeni pa cimene Baibulo ikulankhula kwa ife. Kutipanga kuti tikhale kwa muyaya mu Ufumu Wake, Mulungu analora inu ndi ine kuti tibadwe mwatsopano pomvera uthengau oona, ndiponso Iye anatiombola kuchoka ku machimo athu onse ndi ku chiweruzo. Ndiyamika ndi kuthokoza Ambuye anthu cifukwa cha chipulumutso Chake. 

Ndi mwa mwai kuti mwaufulu tinalandira chikhululukiro cha machimo athu. Onse ndife anthu amene anadalitsika kwakukulu ndi Mulungu. Ndipo ndife aneneri Ake. Choncho, tiyenera kufalitsa uthenga wa chikhululukiro cha uchimo ku miyoyo yonse imene ikalibe kumvapo uthengawu, ndi kulalikanso ku iwo Mawu a Chivumbulutso, kutsilizitsa kwa uthenga. 

Ndiyembekeza ndi kupemphera kuti wina aliyense akhulipilire mwa Yesu, amene ndi Mlengi, M’pulumutsi ndiponso Mweruzi, ndipo, ngati nthawi zomaliza zabwera, choncho n’kulowa malo woyera a Kumwamba kwa Tsopano ndi Dziko lapansi kopatsidwa ndi Ambuye. Lekani kukoma mtima kwa Ambuye Yesu kukhala ndi inu nonse.