Sermons

【3-10】 KODI TCHIMO LOYAMBA LA ANTHU NDI CHIANI?<Marko 7:20-23>

“Ndipo anati, Coturuka mwa munthu ndico cidetsa munthu. Pakuti m’kati mwace mwa mitima ya anthu, muturuka maganizo oipa, zaciwerewere, zakuba, zakupha, zacigololo, masiriro, zoipa, cinyengo, cinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa: zoipa izi zonse zituruka m’kati, nizidetsa munthu.”Pamene tikumvetsetsa za anthu, timazindikira kuti anthu onse ndi odzala ndi uchimo. Anthu ndi mbeu ya zonyansa zimene sangakwanitse koma kuchimwa moyo wao onse. Choncho anthu amachita tchimo lodzala ndi zonyansa, kudzikuza, maganizo oipa, udani, kupha, kuba ndi mitundu yonse ya zoipa za machimo. Kodi mungakhulupirire ngati ndakuuzani kuti anthu ndi omwe amachita zimenezi? Kodi mukukhulupilira kuti anthu ndi achinyengo komanso akuba kwambiri? Kodi mungakhulupilire ngati ndakuuzani kuti anthu ndi omwe amachita chigololo? Kodi mungakhulupilire n’takuuzani kuti munali anthu wotere?

Anthu onse oterewa ndi anthu. Kodi mukukhulupilira m’mau a tchimo lachibadwidwe loyamba mogwirizana ndi malembo omwe akunena kuti anthu onse amabadwa ndi machimo oipa komanso kuchita zodabwitsa zoipa zauchimo? Thupi la anthu limangochimwa moyo onse. Si kukokomeza kunena kuti thupi la munthu ndi fakitale lopanga tchimo. Thupi la munthu limakhala pa uchimo umene Mulungu amadana nao ngati chakudya cha masiku onse. Thupi la munthu limakondwera kuchita tchimo; limasangalala kuchita chigololo, tchimo la zonyansa, ndi kuchita zosemphana ndi Mulungu.

Thupi la munthu limachimwa kuchoka kubadwa mpaka pa nthawi lakufa kwake. Sikuti thupi la munthu limakondwera ndi kuchita uchimo okha, koma limakondweranso kutisatira zokhumba za thupi lake. Yesaya 1:4 akuti anthu ali “mbeu yakucita zoipa,” komanso Yesaya 59 akunena kuti pali mitundu yonse ya zonyansa komanso za manyazi m’kati mwa mtima wa munthu. Choncho, munthu ndi mulu wa uchimo. Ndiyeno, ngati tatenga kuchokera ku mau a Mulungu kuti “munthu ndi mulu wa uchimo,” kenako, tiyenera kulandira mauwa a Mulungu mu mtima mwathu. Ndipo tiyenera kuzindikira pamaso pa Mulungu kuti ndife anthu ochimwa chotere ndipo kenako tidikire maphunziro a Yesu. 

Anthu ndi onyansa. Pamene munthu waziona yekha bwino bwino, angathe kupeza kuti iye ndi onyansa ndipo zonyansazo ndiye umunthu wake. Munthu amene ali wachilungamo pa iye yekha angabvomereze kuti munthu ali ndi mitundu khumi ndi iwiri ya machimo imene Mulungu akukambapo. Ngakhale ziri choncho, sizikuonetsa kwa anthu ambiri amene amazindikira kuti iye yekha ndi onyansa, kuti iye ndi mulu wa uchimo. Anthu ambiri amakhala monga chirombo m’dziko lino chifukwa samaganiza kuti ndi onyansa.

 Anthu amazipangira chikalidwe cha zonyansa chifukwa anthu ali “mbeu yakuchita zoipa.” Munthu akanakhala wamanyazi ngati iye yekha ndiye onyansa m’dziko kuchita makhalidwe onyansa, koma iwo anapanga zonyansa chikhalidwe kuti asakhale amanyazi chifukwa ali yense ndi onyansa. Komabe, mtima wa munthu ali yense umamva manyazi mu chikumbumtima chake pa khalidwe lake la uchimo. Ndi chifukwa chakuti Mulungu anapereka chikumbumtima kwa anthu. Chikumbumtima cha munthu ndi kapolo wa Mulungu amene Iye anatuma ngati wachiwiri Wake.

Adamu ndi Hava anabisala pakati pa mitengo pamene anachimwa. Mitengo yambiri ikutanthauza munthu amene waphimbidwa ndi chikhalidwe chonyansa. Komabe, sangabise kuipa mu mtima mwao. Ngakhale tsopano, ambiri omwe ndi mulu wa uchimo amaenda m’kati mwa anthu ambiri ndi kudzibisa okha m’kati mwa chikhalidwe cha machimo oipa ndi kukhala monga mkaidi wodikirira kuphedwa.Ali yense amakhala ndi kusazimvetsetsa yekha


Anthu amakhala ndi kusazimvetsetsa iwo okha. Pamene chodabwitsa ndi chonyansa chachitika, pali anthu ambiri amene amafunsa nanga munthu angachite zinthu zotere komanso nanga mwana wa mwamuna kapena wamkazi angachite zinthu zoopsa zotere kwa makolo ake. Ndipo iwo amati sali otere kuchiyambi ngakhale anthu onse ali choncho. Koma, anthu ndi zolengedwa zomwe si zingazimvetsetsedi. Ndipo kuti munthu azimvetsetse yekha bwino bwino, iye ayenera kubwera pamaso pa Uthenga Wabwino oyamba ndi kubadwa mwatsopano mwa mau oyamba a Uthenga Wabwino wa nzeru.

Pali anthu ambiri mdziko lino amene amwalira osadziwa zoonadi zeni zeni za iwo okha mpaka kufa. Pamene tikuyang’ana pa dzikoli mwatcheru, pali zodabwitsa zambiri zochitika. Pamene tikuyang’ana anthu mwacheru, tikhonza kuona kuti pali anthu ambiri amene amadzionetsa ngati olungama. Pamene munthu wina akulankhula zamanyazi, iwo amati “nchiani mdziko chimenecho!” zingatheke bwanji mbuli kulankhula zimenezi? Iwo amati munthu sakuyenera kunena zotero ngakhale munthu akuloza chinthu choipa. Iwo amati tiyenera kuitana wakuba “bambo wakuba.” Ichi ndi chinyengo komanso mwano.Mulungu akuti, “zidziweni nokha”


Pamene tikuyang’ana pa munthu otere, ndadziwa kuti munthu ameneyu samazidziwa yekha. Ngakhale azaumoyo amati, “zidziwe wekha,” anthu samazidziwadi okha mkomwe; samadziwa kuti ndi machimo otani amene anasungidwa mwa iwo. Uthenga Wabwino wa Marko mutu 7 ndime 21-23 ananena kuti pali mitundu khumi ndi iwiri ya machimo m’kati mwa mtima wa munthu pa chiyambi. Mtima wa kupha, mtima wachilakolako, mtima wa nsanje, mtima wa umbava, mtima wa maganizo oipa, mtima opusa ndi machimo ena ambiri mkati mwao, koma ndaona iwo akukhala osadziwa kuti iwo okha ndi achinyengo komanso kuti akungolankhula mau odzibisa abwino ngakhale ali poizoni wa njoka mkati mwa mitima yao. Ichi n’chifukwa chakuti samazidziwa okha.

Pali anthu ambiri m’dziko lino amene samazidziwa okha. Choncho, pali anthu ambiri amene agwera mu gahena podzinyenga okha ndi kukhala moyo wao onse pongodzinyenga okha ndipo posakhulupilira muchipulumutso cha Uthenga Wabwino oyamba. Pali anthu ambiri amene akupita ku gahena podzinyenga okha pachiyambi. Pamene anthu ena akupita ku gahena atakhala m’dziko lino, mwana mfumu wa Hadesi wafunsa, “kodi n’chifukwa chiani mwabwera ku gahena?” ndipo anthuwo angayanke kuti, “ndi maganiza kuti mwina ndingapite kumwamba ngakhale kuti ndimaganiza kuti bambo akuti akuti amene ankakhala pakhomo lachiwiri angabwere kuno. Sizachilungamo kuti ndabwera kuno.” Iwo angaganize kuti, “ine ndimaganiza kuti ndiliko bwino pang’ono kuposa anthu ena. Sindikuziwa chomwe ndabwerera kuno.” Anthu omwe samazidziwa okha komanso samadziwa ndi kukhulupilira mu Uthenga Wabwino oyamba wa chipulumutso amapita ku gahena.

Kodi munthu ndi chiani? Monga m’mene ndanenera kale pachiyambi, munthu ndicholengedwa chonyansa. Munthu ndi mbeu ya “mbeu yakuchita zoipa.”

Zikuoneka ngati zili bwino kunena kwa ali yense kuti ndi onyansa, koma ngati ndinganene kwa munthu m’modzi kuti “ndiwe munthu onyansa,” iye angalongedze ndikuchoka pamalo ano mwachangu. Koma ngakhale ndaloza munthu wina ndi kunena kuti, “ndiwe mulu wa uchimo ndipo ndiwe munthu onyansa,” izi zingakhale zoona kotheratu. Tonse ndi chimodzi modzi pamaso pankhope ya Mulungu. Pamene munthu wamva kuti munthu ndi mbeu yazochita zoipa kuchokera pachiyambi, iye amangoganiza, “oh, zili choncho,” ndipo amamvera mosafuna monga ndi za anthu ena. Koma, ngati mwayankha, “inde, ndine,” pamene mwauzidwa, “ndinudi munthu otero,” ndiye kuti, ndinu munthu wachilungamo. Komabe, pali anthu ambiri amene amawiringula ndi kupatsa mlandu anthu ena. Munthu otero ndi mbuli ya munthu amene sangathe kuziona yekha. Iye yekha, inu nokha, komanso ine ndekha ndi mulu wa uchimo. Ndife “mbeu yakuchita zoipa amene sitingakwanitse koma kukhala onyansa pachiyambi.” Tinafunikira nzeru ya Uthenga Wabwino oyamba wa Yesu chifukwa ndife onyansa a mbeu yauchimo, koma ngati sichoncho, ngati tikanakhala ndi zolakwa chabe ndipo sitinali a mbeu ya zonyansa, n’chifukwa chiani tikanafuna nzeru ya Uthenga Wabwino oyamba wa Yesu? Yesu sakanabwera padziko lino tikanakhala kuti sindife oipa pachiyambi.Anthu amataya machimo nthawi ili yonse chifukwa ndi ochimwa mwachibadwidwe 


Machimo adzadza mu mtima mwa munthu, mkati mwa mzimu. Tiyeni tinene kuti madzi mkati mwa kapu ndi tchimo la munthu mu mtima ndipo kenako, uchimo mkati mwa kapu ungataikire pamene munthu akuzungulira pamene akukhala m’dziko lino, Kodi sichoncho? Ungataikire paliponse. Umataikira paliponse pamene munthu akudzandima kuno ndi uko. Anthu amapita kuzungulira dziko lonse kutaya machimo motere moyo wao onse. Anthu amachimwa pamene akukhala m’dziko lino chifukwa ndi mulu wa uchimo.

Anthu sadziwa bwino bwino kuti ali ochimwa motani. Ngakhale ndife anthu amene tili ndi mtima wa uchimo monga mulu wa uchimo moyo waao onse, timaganiza kuti, “ndilibe zilako lako kuchokera pachiyambi. Ndakhala chonchi chifukwa wina anandikankhira ku chilakolako. Sindine munthu onyansa kuchokera pa chiyambi. Ndikufunika kungochotsa machimo onyansa ndachitawo basi. Iwo amati “sindine onyansa kuchokera pachiyambi!” ndipo amachotsa mobwereza bwereza ndi ntchito zabwino kapena mapemphero akulapa pamene uchimo wao waonekera kunja. Kodi uchimo sumataika kawiri kawiri pamene mwauchotsapo? Umataikabe paliponse. Chifukwa m’kati mwa mtima wa munthu ndi modzadza ndi uchimo, amachita uchimo mwachikhalidwenso. Zilibe kanthu kuti munthu wachotsa motani kunja kwake. Zilibe kanthu kuti munthu watsuka kunja (ntchito) mwa khalidwe kapena mwamchitidwe, ndi zopanda ntchito ngati ali ndi uchimo mu mtima mwake. Munthu amachimwa moyo wonse ndi mtima wakupha, mtima wachigololo, mtima waumbava ndi zina zotero. Choncho, anthu amachita machimo ambiri apa ndi apo moyo wao onse.Anthu amayesa molimba kudzibisa okha pamene asakuzidziwa okha 


Anthu amayesa molimba kudzibisa okha akakhala kuti sakudziwa kuti ndi mulu wa uchimo mwachibadwidwe. Tiyeni tinene mwachitsanzo, uchimo m’kati mwa mtima wa munthu wataika pang’ono. Iye amataya uchimo ochuluka pamene watsuka uchimowo, ndipo ayenera kuchotsa uchimowo pafupi pafupi ndi kachopukutira. Kenako, pamene sanakhutire, iye ayenera kuchotsa mobwereza bwereza ngakhale ndi chinsalu chachikuru, ndipo zingakhale zodabwitsa ngati munthu sanachimwenso atatha kukonza vuto la uchimo, koma samakhala oyera ngakhale angatsuke bwanji kuyenderera kwa uchimo. Timagwa mu uchimo mpaka nthawi yakufa kwathu. Anthu ndi omwe amachita khalidwe lonyansa mpaka kufa. Choncho, munthu amene amachimwa ayenera kulandira Yesu monga mpulumutsi amene anampulumutsa iye ku machimo pofuna kulandira chipulumutso. Ndipo polandira chikhululukiro cha machimo, munthu ayenera kudziwa chiyambi chake monga zilili.

Tiyeni tinene kuti pali anthu awiri amene ndi machimo ofanana m’kati mwao ngati makapu awiri ofanana odzadza ndi madzi. Wina wadziona yekha ndi kuganiza, “ndine mbeu yonyansa mwachibadwidwe,” ndipo kenako amaleka kuyesa kudzikonza yekha ndipo amayang’ana kuti apeze mpulumutsi. Pamene munthu winayo samaona mulu wa uchimo mkati mwake ndipo amaganiza, “ndine wapamwamba.” Munthu amene akukhulupilira kuti iye ndi wapamwamba amatsuka uchimo wake mpaka tsiku lakufa kwakwe. Ndipo amasamalitsa kuti machimo asataikire ndi kuyenderera, ndipo moyo wake onse amayesera kubisa chibadwa chake cha mulu wa uchimo kubisa uchimo otaikira apa komanso kubisa uchimo otaikira apo.

Monga chonchi, pali anthu amene amakhala mosamalitsa pa kuopa uchimo kuyenderera pamene akukhala moyo wao odzadza ndi machimo onyansa m’kati mwa mtima wake. Kukhala mosamala sikungathandize kwenikweni kuti apite kumwamba chifukwa ali nao kale mulu wa uchimo m’kati mwao, koma sadziwa kuti kukhala mosamala chotero chakhala mapazi akugahena. Adzapitabe kugahena ngakhale anakhala mosamalitsa. Munthu amene amakhala mosamalitsa ndi ochimwa amene amachita mitundu yonse ya machimo mobisa ngakhale mulu wake wa uchimo sumataikira kwambiri.

Kodi mukubvomereza kuti munthu ali ndi mtima onyansa, maganizo oipa, mtima waumbabva, mtima odzikuza m’kati mwa mtima wa munthu? Tingadziwe kuti munthu ndi mbeu yonyansa pongoona anthu kuchita machimo onse onyansa ngakhale palibe omwe anawamphunzitsa. Munthu sadziwa bwino pamene ali mwana chifukwa samaonekera kwambiri, koma palibe njira iliyonse yobisila mulu wa munthu wa uchimo pamene iye akukula. Munthu sangadzithandize koma kutaya machimo ake mowirikiza. Amaonetsa uchimo apa pang’ono ndi apo pang’ono, ndipo kenako amadzitsutsa. Iye amadzitsutsa, kunena kuti “sindimayenera kuchita choncho,” koma kupitiliza kutaya uchimo moyo wake onse ngakhale amadzitsutsa tsiku lililonse monga choncho. Iye ali choncho chifukwa anabadwa ndi mulu wa uchimo. 

Ndikunena kuti munthu angalandire chikhululukiro changwiro cha machimo chimene Ambuye amapatsa pokha pokha ngati iye wadziwa kuti ndi mbeu yakuchita zoipa mwachibadwidwe. Munthu amene amazidziwa yekha kuti iye ndi mulu wa uchimo pamaso pa Mulungu angakhulupilire popanda kunyalanyaza ngati munthu wina wamuuza kuti Yesu anafufuta machimo ake onse pochita ntchito yolungama yotere ndi yotero. Koma, munthu amene akunena kuti, “ndachita tchimo ili lokha kufikira tsopano ndipo sindinachitepo machimo ambiri,” angakane mokhazikika ndi kusakhulupilira mu choonadi choti Yesu anachotsa machimo ake onse Iye yekha polandira ubatizo ndi kunyamula machimo onse kupita nao pamtanda. Koma, munthu amene akufuna kupulumutsidwa amalandira chikhululukiro cha machimo pokhulupilira kuti ndi mulu wa uchimo otheratu komanso pokhulupilira m’Mau a choonadi kuti Ambuye anakonza bvuto la machimo onse pamtanda mwa ngwiro pamene analandira ubatizo pa mtsinje wa yordano.

Ndikunena tikukhala ndi kusamvetsetsa kwakukuru mwa ife tokha kupatura kuti wina analandira chikhululukiro cha machimo kapena ai. Tilibe uchimo ngati Ambuye wathu anafafaniza machimo onse a anthu mwa ubatizo Wake ndi mwazi ndipo timalandira chikhululukiro cha machimo ngati takhulupilira zimenezo. Choncho, Mulungu anapanga pangano la tsopano, kunena, “taonani, masiku adza, ati Yehova, ndipo ndidzapangana pangano la tsopano ndi nyumba ya Israyeli, ndi nyumba ya Yuda” (Yeremiya 31:31). Zikutanthauza kuti Mulungu azakhazikitsa pangano la tsopano m’malo mwa pangano la kale. Pangano la tsopano linali chifuniro cha Mulungu kuti Ambuye Yekha adzabwera pa dziko lino ndi kupulumutsa ochimwa oipa pothenga ndikufufuta machimo onyansa moyo wao onse. Linali pangano la tsopano limene Mulungu adzapulumutsila anthu amenewa ndi kukhala Mulungu wao. Iye anati, “ndidzachotsa machimo onse onyansa pa anthu ndikukhala Mulungu wao komanso adzakhala anthu anga.” Pangano la tsopano likupitiliza kunena kuti, “ndipo sadzaphunzitsa yense mnansi wace, ndi yense mbale wace, kuti, mudziwe Yehova; pakuti iwo onse adzandidziwa, kuyambira wamng’ono kufikira wamkuru wa iwo, ati Yehova; pakuti ndizakhulukilira mphulupulu yao, ndipo sindidzakumbukira cimo lao” (Yeremiya 31:34).

Pangano la tsopano la Mulungu ndi lakuti sitingakhale olungama posunga lamulo pakuti sitingakhale olungama poyesera kusunga lamulo. Akatswiri azamalamulo akuchita machimo ambiri mobwereza ndipo akupempha Mulungu, “Ambuye, yeretsani machimo anga. Ndachita cholakwika tsiku la lero. Ndiyeretseni ine, Ambuye, ndiyeretseni ine, chonde” ichi ndi chikhulupiliro cha chilamulo. Mu ndondomeko yakaperekedwe ka nsembe ya Chipangano chakale, munthu ankayenera kupereka machimo a tsiku ndi tsiku poika manja ake pamutu pa mbuzi kapena mwana wa nkhosa komanso ankapereka machimo a chaka chonse poika manja a mkuru wansembe, ndipo iwo kenako ankapitiriza kupereka nsembe, koma munthu anali ochmwabe ngati iye wachitanso tchimo. Choncho, kukhululukidwa kwa uchimo kosatheka mwa lamulo. Motero, pangano la tsopano la Mulungu linayenera kwa ochimwa aliyense, monga Ambuye ananena kuti, “sindinadze Ine kuitana olungama, koma ochimwa kuti atembenuke mtima.” Mulungu anaganiza zokhala ndi anthu onyansa chotere monga mkazi wa Hoseya monga mkazi Wake. Monga mwachitsanzo ndapereka kumbuyo, anthu onse awiri ndi odzadza ndi machimo. Onse anabadwa ndi thupi lofanana ndi machimo ofanana. Koma wina amakhala mosamala pofuna kusataya machimo; iye amakhulupilira mwa Yesu mosamalitsa. Izi zikutantauza kuti anthu ena amasamala za kusefukira kwa machimo ao. Ndipo pamene dontho la tchimo lataika, amapereka mapemphero akulapa kuti atsuke tchimolo, ndikunena kuti, “Ambuye ndachita tchimo lero.” “chonde ndikhululukireni tchimo limeneli lokha.” Amaziyeretsa ndi kukhulupilira malingana ndi kuchuluka kwa kulapa kwao. Iwo ndi ochimwabe mkati ndipo amakhala odandaula ngakhale amaoneka ngati ndi aKristu abwino muchinyengo kunja. 

Okondedwa anzanga okhulupilira, ndife anthu onyansa. Inu ndi ine tiyenera kuziwa kuti ndife anthu opita ku gahena. Pokhapo, ndife othokoza kuti Ambuye anachotsa machimo athu onse ndipo ndife oyamikira polandira chikhululukiro cha machimo pamene machimo athu ataika komanso pamene takumbukira choonadi chakuti Ambuye anatipulumutsa ife mbeu yonyansa chotere. Tingakhale othokoza tsopano. 

Pali akaidi ambiri achinyengo pakati pa anthu omangidwa. Pakati pa iwo, ena analamulidwa kukaphedwa pamene ena analamulidwa kukhala moyo wao onse ku ndende. Ndipo pali mitundu yambiri ya ochimwa amene anamangidwa chifukwa cha umbanda, amene anamangidwa chifukwa cha umbabva, komanso amene anamangidwa chifukwa cha zolakwa zambiri zodabwitsa. Ndipo pamene ndapita kukalalikira Mau, iwo amati, “abusa, kodi inu simunachitepo tchimo? Tinamangidwa chifukwa tinali ndi tsoka ndipio tinagwidwa, koma inu, abusa mukukhala kunja tsopano chifukwa mumachimwa mobisa ndipo simunagwidwepo. Kodi mukuganiza kuti ndinu abwino kuposa ife? N’chifukwa chiani akutitsekera ife chonchi? Ndi tchimo lotani lomwe tinachita tikafananiza ndi anthu onse?” Monga chonchi, akaidi saganiza kuti anachimwa.

Kukamba motsindika, iwo akunena zoona. Ngakhale sitinamenye munthu wina mpaka kufa, tili ndi udani ndi anthu mu mtima mwathu. Kenako chimodzimodzi monga kupha m’maso mwa Mulungu. Izi zikutanthauza kutikapena wina aphe munthu kapena ade munthu, onse ali ndi tchimo lofanana m’maso mwa Mulungu. Amanena kuti Mulungu amayang’ana pakati pa mtima wa munthu, osati kunja kwake. Ndiyeno, ifenso timayenera kumangidwa.

Pamene tinali kupita kumunda kale kale, kunali manyowa otchingidwa ndi mphasa zaudzu. Pokha pokha munthu achotse mphasayo, manyowa sangaoneke. Anthu naonso ndi onyansa monga chonchi; pamene tachotsa chobvindikira cha ntchito za chilungamo za anthu ubwino komanso kunyada, kulibe cholengedwa monga chonyansa ngati munthu wamachimo ambiri. Pali mitundu yonse yamachimo mkati mwa munthu pamene tachotsa chobvindikira kotheratu ndi kuyang’ana m’kati pamaso pa Mulungu. Koma Ambuye wapanga munthu amene amabvomereza moona, “ndine munthu otere,” monga munthun olungama kudzera muchipulumutso cha Uthenga Wabwino oyamba malingana ndi pangano lake latsopano. 

Tiyenera kudziwa kuti tinalandira chikhululukiro cha machimo chifukwa cha chilungamo cha Mulungu. Talandira chikhululukiro cha machimo chifukwa cha chilungamo cha ubatizo omwe watipatsa ife chipulumutso chenicheni cha Yesu. Palibe angalandire chikhululukiro cha machimo mwa chilungamo chake. Munthu amene akuonetsa ntchito zake zabwino ndipo sakhulupilira mu chilungamo cha Mulungu sangalandire chikhululukiro cha machimo. Munthu amene alibe chilungamo cha iye yekha amalandira chikhululukiro cha machimo pobwera pamaso pa Ambuye ndi kukhulupilira muchilungamo chimene Ambuye anapereka. Mulungu sanapulumutse “ochimwa pang’ono”


Mulungu sapulumutsa “ochimwa pang’ono.” Izi zikutanthauza kuti Mulungu sayang’ana mkomwe pa munthu amene amanena kuti “Mulungu, ndili ndi machimo ochepa.” Ndiyeno, ndindani amene Mulungu amasamala? Mulungu amayang’ana pa anthu amene akhala ochimwa kotheratu amene akuti, “Mulungu, ndikupita ku gahena. Ndine mulu wa machimo otheratu. Mulungu, chonde, ndipulumutseni.” Mulungu amapulumutsa munthu amene wadzipereka yekha kwa Ambuye kotheratu ndi kupemphera, “Ambuye, ndidzalandira chipulumutso pamene Inu mwandipulumutsa, ndipo ndidzapita ku gahena ngati Inu simudzandipulumutsa ine. Sindingapempherenso mapemphero akulapa. Ndidzachimwanso ngakhale nditapemphera mapemphero akulapa. Ambuye, chonde, ndipulumutseni.”

Munthu sangazembe uchimo popemphera mapemphero akulapa. Munthu amene amanena, “Mulungu, ndichitileni chifundo ine komanso ndipulumutseni ku machimo anga,” angalandire chipulumutso pokhulupilira chimene Yesu anatetezera machimo athu onse kotheratu potenga machimo pa Iye yekha kudzera mu ubatizo umene analandira kwa Yohane Mbatizi.

Kunalembedwa m’Buku la Yesaya 59:1, “Taonani, mkono wa Yehova sufupika, kuti sungathe kupulumutsa; khutu lace siliri logontha, kuti silingamve.” 

Mulungu saona anthu monga chobvomerezeka chifukwa iwo ndi mulu wa uchimo kuchibadwidwe. Mulungu samaona munthu kubvomerezeka ngati iye ali ndi tchimo limodzi kapena awiri, koma Mulungu sayang’ana pa munthu otereyu chifukwa ali yense ndi mulu wa uchimo. Mau m’Buku la Yesaya akuti mkono wa Mulungu sufupika kuti sungathe kupulumutsa ndipo kuti makutu ake siogontha kuti sangamve mau onena kuti, “chonde ndikhululukireni machimo anga.” Mulungu akuti, “Koma zoipa zanu zakulekanitsani inu ndi Mulungu wanu; ndipo machimo anu abisa nkhope yace kwa inu, kuti iye sakumva” (Yesaya 59:2), ndipo zikutanthauza kuti ngakhale Mulungu watsegula madalitso a kumwamba, khomo la kumwamba, palibe angalowe chifukwa anthu ali ndi machimo ambiri m’maso mwa Mulungu.

Ngati munthu amene ndi mulu wa uchimo anakhululukidwa pazolakwa zina zimene iye anachita nthawi ili yonse popemphera mapemphero akulapa, ndiye kuti, Mulungu amayenera kupha Mwana Wake nthawi ili yonse munthu wapemphera chikhululukiro cha machimo ake. Koma, Mulungu sakufuna kupha mwana wake mobwereza bwereza. Choncho, Mulungu anati, “musamabwere kwaine ndi machimo amene mumachita tsiku ndi tsiku. Ndipo m’malo mwake ndidzatuma Mwana Wanga kuti akupulumutseni kumachimo anu onse pochotseratu machimo anu onse. Choncho, mvetsetsani m’mene Mwana Wanga anachotsera machimo anu onse amene muchimwa ndikuona kapena izi ndi zoona kapena ai ndi kulandira chikhululukiro cha machimo pokhulupilira mu Uthenga Wabwino wachipulumutso omwe Mwana Wanga anakwaniritsa kwainu. Ichi ndi chikondi chachikulu.” Iye akuti, “landirani chipulumutso pokhulupilira mwa Mwana Wanga. Ine, Yehova Mulungu, ndidzatuma Mwana Wanga ndi kufafaniza milu yonse ya machimo, machimo onse a tsiku ndi tsiku, ndi mphulupulu zonse za anthu onse. Khulupilirani mwa Mwana Wanga ndikulandira chipulumutso ku uchimo wanu omwe ndi mulu wa machimo.”

Malembo akunena za mitundu ya machimo yomwe ili mkati mwa mtima wa munthu. Tiyeni tiwerenge Mau kuchokera m’Buku la Yesaya 59:3-8 “Pakuti manja anu adetsedwa ndi mwazi, ndi zala zanu ndi mphulupulu, milomo yanu yanena zonama, lilime lanu lilankhula moipa. Palibe woturutsa mlandu molungama, ndipo palibe wonena zoona; iwo akhulupirira mwacabe, nanena zonama; iwo atenga kusayeruzika ndi kubala mphulupulu. Iwo afungatira mazira a mamba aswetse, naluka ukonde wa tandaude; iye amene adya mazira ace amafa, ndi coswanyikaco cisweka nicikhala songo. Maukonde ao sadzakhala zobvala, sadzapfunda nchito zao; nchito zao ziri nchito zoipa, ndi ciwawa ciri m’manja mwao. Mapazi ao atamangira koipa, ndipo iwo afurumira kukhetsa mwazi wosacimwa; maganizo ao ali maganizo oipa; bwinja ndi cipasuko ziri m’njira mwao. Njira ya mtendere saidziwa, ndipo palibe ciweruziro m’mayendedwe mwao; akhotetsa njira zao; ali yense ayenda m’menemo sadziwa mtendere.”

Kunalembedwa, “Pakuti manja anu adetsedwa ndi mwazi, ndi zala zanu ndi mphulupulu.” Izi zikutanthauza kuti munthu amachimwa moyo wake onse. Chili chonse chomwe munthu achita ndi tchimo. Kachiwiri, kunalembedwa, “milomo yanu yanena zonama.” Izi zikutanthauza kuti chili chonse chimene munthu alankhula ndi chabodza. Mulungu akuti, “Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wace” (Yohane 8:44). Anthu amene sanabadwe mwatsopano amanena zinthu monga, “ndikunena zimenezi moona,” kapena “zoonadi ndi kukuuza.” Iwo amagwira mau “moona” kapena “zoonadi” kuchili chonse akamba, koma zonse ndi zabodza ngakhale anganene moona kapena ai. Mau olembedwa akuchitira umboni kuzimenezi, monga kwanenedwa, (Pamene iye [mdierekezi] alankhula bodza, alankhula za mwini wace).

Osati munthu wapadera yekha, komanso ali yense ali chonchi. Machimo amasefukira kwa munthu mosasamala. Ichi n’chifukwa ali yense ndi mulu wa uchimo. Koma mphamvu ya Mulungu ndi yodabwitsa; ndi mphamvu ya Mulungu imene munthu amene ndi mulu wa uchimo chotero amalandira chipulumutso ku machimo. Uchimo umasefukira pamene munthu wakwiya komanso wakhumudwa, ndiponso uchimo umayendelera mosalamulirika ngakhale mtima wa munthu uli ndi mtendere komanso thupi lili paufulu. Uchimo umasefukira motero posatengera mkhalidwe. Koma chodabwitsa n’chakuti ngakhale ochimwa otere amene tchimo lake likusefukira angalandire chipulumutso kumachimo kuchokera kwa Ambuye wathu. Ambuye anadza kudzapulumutsa ochimwa otere. Ndikufuna inu kuti muzidziwe nokha ndikulandira chipulumutso cha machimo onse pokhulupilira mwa Yesu amene anadza mwa madzi ndi Mzimu.

Mau mu Uthenga Wabwino wa Marko 7 akutiuza ife kuti tchimo la chibadwidwe la munthu ndi chiani. Anthu ali ndi maganizo ao okhudza tchimo la chibadwidwe. Anthu ena amaganiza kuti zolakwa zao ndiye tchimo la chibadwidwe. Chifukwa anthu ali ndi maganizo ao paokha okhudza tchimo, anthu agwera mu chisokonezo posadziwa tchimo la chibadwidwe la anthu komanso machimo a tsiku ndi tsiku. Choncho, tiyenera kukambilananso pa za m’mene ali yense wagwera mu chisokonezo.

Tiyeni tione mwachitsanzo posiyanitsa muyezo wa tchimo pakati pa khalidwe mu Papua New Guinea ndi mu Korea. Mu Korea, pamene makolo afa zimafunika mwambo olemekeza wa ana amuna kapena akazi kuwakwirira pansi ndi kudula maudzu pamwamba pa mtumbila pafupi pafupi pasanathe chaka ndi kusamalila mtumbilao pamene adakali moyo. Koma, mu Papua New Guinea, pamene makolo afa mitundu ina imatsata mwambo kuti ana ao akhale mozungulira mtembo ndi kudya thupi la mtembowo. Amachita choncho pofuna kuteteza mtembowo kunyama zolusa kapena ku nsikidzi. Choncho tingathe kuona kuti lingaliro la anthu pa mwambo olemekeza wa ana ndi lingaliro la tchimo n’zosiyana.

Komabe Mulungu akunena m’malembo pa machimo obadwa nao a munthu monga chonchi: mitundu khumi ndi iwiri ya chilengedwe cha uchimo yomwe ndi chizolowezi chochita tchimo limene munthu anatenga kuchokera ku makolo komanso machimo amene munthu amachimwa pamene akukhala mdziko lino ndiwo machimo a munthu.Tchimo lomwe Ambuye analankhula kwa anthu okhulupilira mwa Ambuye


Kwa anthu amene akhulupilira mwa Mulungu, Ambuye akuti kusakhulupilira mu Mau a Mulungu ndi kuwataya ndi tchimo. Ambuye akuchenjeza ndi kudzudzula mwa mphamvu okhulupilira mwa Yesu amene ali ngati Afarisi, kunena kuti, “muyenera kukhulupilira mu Mau anga a madzi ndi Mzimu, Mau achipulumutso ku machimo, popanda kuchotsapo choona ngakhale chimodzi ku Mauwo.” AKristu onse ochimwa kuphatikizanso okhulupilira zipembedzo komanso azipembedzo amipingo yosiyana sakhulupilira mu Mau a Mulungu chifukwa anasankha kukhulupilira m’mau a azitsogoleri ao achikhulupiliro komanso azipembezo a mipingo yao, mau a azibusa akulu akulu amene ali ndikhalidwe lolemekezeka komanso umphumphu kuposa Mau olembedwa a Mulungu. Iwo akunena kuti mau ao ndi achiphunzitso cheni cheni. Ambuye akudzudzula okhulupilira chipembedzo otere.

Monga chonchi, Ambuye amaona kusakhulupilira kotereku ngati tchimo lachikhalire. Choncho, pamene Iye waona Afarisi, iwo anali ochimwa oteratu amene anali apamwamba mu chinyengo. Choncho, Ambuye anawadzudzula iwo ngati onyenga ndikunena kuti, “ndi mulungu wotani amene mukhulupiliramo? Kodi mumafunitsitsadi, kukhulupilira, ndi kulemekeza Ine? Mumadzikuza mwa Ine, Yehova Mulungu, koma mumakhulupiliradi mwa Ine? Kodi kulemekeza Ine ndi chiani? Mumakhulupilira mwa Ine kunja kokha.” Tiyenera kumvetsetsa kuti Mulungu anadzudzula izi ngati tchimo lalikuru m’maso mwa Mulungu.

Tchimo lalikuru limene likupezeka mdziko ndi tchimo la kunyala nyaza Uthenga Wabwino wa Mau a nzeru yeni yeni yakubadwanso mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu yomwe inalembedwa m’malembo a Mau omwe Mulungu anakamba kwa anthu. Mwanjira ina, ndi tchimo la kusakhulupilira mu choonadi cha chipulumutso ndi mtima. Pakati pa machimo onse, Mulungu akuti tchimo la chinyengo ndi la kugahena ndi tchimo losakhulupilira Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu omwe unafufuta machimo onse a ochimwa adziko lonse; Uthenga Wabwinowu unakwanilitsidwa ndi Ambuye polandira ubatizo, kufa pamtanda, ndi kuukanso kwa akufa. Kwa munthu amene akhulupilira mwa Yesu, kusakhulupilira m’Mau a Mulungu m’malo mwake kuwataya ndi tchimo la ku gahena, osati chinthu china. Ndipo zochita zolakwika zomwe tachita mwa kufooka, kulakwitsa komwe timapanga, amatchedwa machimo a mphulupulu m’malembo.

Mulungu anagawa machimo obadwa nao a anthu ndi machimo a tsiku ndi tsiku, ndipo Ambuye wathu anadzudzula Afarisi ndi Alembi monga achinyengo chifukwa chosazindikira Mau a Mulungu kwapangitsa iwo ochimwa akulu pamaso pa Mulungu ngakhale kuti sanaphwanye lamulo pamaso pa Mulungu. M’mabuku oyamba a Chipangano chakale, tikoza kuona kuti pali malamulo ambiri a “chitani komanso musachite.” Mau onsewa ndi lamulo limene Mulungu analamula kwa anthu. Ngakhale sitingasunge Mau a Mulungu mwa ngwiro chifukwa cha kulephera kwathu kosunga Mau, tiyenera kuzindikira lamulo la Mulungu ngati momwe Mau a Mulungu amazindikilira, “awa ndi Mau amene Mulungu analankhula kwa ife,” ndipo tiyenera kuzindikira Mau onse olembedwa m’malembo ngati Mau a achisomo ndi lamulo la Mulungu chifukwa onse ndi Mau amene Mulungu anatilamula ife. Ndipo tiyenera kukhulupilira kuti “Mau a Mulungu ndilo lamulo, komanso moyo.” Mulungu anapanga akapolo ake kulemba Mau amene Mulungu analankhula ndi kutiuza ife anthu kukhulupilira mwa Mauwo.

Kodi ndindani analemba Mau a malembo? Mulungu analemba Mau ake kudzera mu akapolo ake amene anadzadzidwa ndi Mzimu Woyera. Monga Mulungu anati, “Ndine Yehova.” Izi zikutanthauza kuti Mulungu ndi Mulungu opezeka-yekha ndipo Iye sanalengedwe ndi ali yense. Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi monga kunalembedwa, “pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi” (Genesis 1:1). Patatha izi, panali kuunika pamene Mulungu anati, “kuyere,” ndipo Iye analenga dziko lonse ndi zonse m’menemo, kukhazikitsa lamulo la chipulumutso mwa Mau a ndondomeko ya kaperekedwe kamsembe omwe Iye analankhula, ndipo Mau anasandulika thupi ndipo anaonekera pakati pathu, ndipo Yesu ameneyu anali Mulungu kuchokera pa chiyambi. Yesu anaonekera yekha chimodzi modzi monga mwa Mau amene Iye analankhula m’Chipangano Chakale, ndipo Yesu amene ndi Mulungu anakonza Mau amene Iye analankhula ndi kutiphunzitsa ife tonse lamulo la chipulumutso komanso lamulo la chisomo ndi dalitso. Choncho, timakhulupilira m’malembo monga Mau olankhulidwa ndi Mulungu. 

Monga kunalembedwa mu Uthenga Wabwino wa Marko 7:8, “Musiya lamulo la Mulungu, nimusunga mwambo wa anthu,” ndipo pali malamulo 613 amene Mulungu analankhula kwa ife anthu. Analembedwa monga mitundu iwiri ya Mau: chitani komanso musachite; khulupilirani komanso musakhulupilire. Akutiuza ife kuti tikhulupilire mu dalitso la Mau onse monga “lemekeza makolo ako; usaphe; usachite chigololo; usabe; osachita umboni wabodza,” ndi zina zotero. Mulungu anatipatsa malamulo 613 kuuza anthu zoyenera kukhulupilira komanso zosafunika kukhulupilira komanso zoyenera kuchita ndi zosafunika kuchita. Ndi malamulo a Mulungu. Tiyenera kulemekeza zofunika kuchita ndi zosafunika mwa chikhulupiliro chifukwa si mau a munthu koma malamulo a Mulungu. Tiyenera kukhulupilira Mau olembedwa a Mulungu ndi kuwatsata ngakhale tilibe kuthekera kokhala ndi Mau a Mulungu; tiyenera kukhulupilira mu mtima mwathu kuti Mau ake ndi olungama ndi kukhala mwa chikhulupiliro m’Mau.

Kodi pali chili chonse chosalungama m’Mau a Mulungu? Ai, palibe. Koma, Israyeli anataya Mau a Mulungu ndi kusakhulupilira mwa Yesu ngakhale pamene Yesu anadza kwa iwo koma m’malo mwake anamukana Iye. Ndipo anaika mphamvu kwambiri m’mau azitsogoleli ao anthawi imeneyo kuposa Mau a Yesu ndipo mau omwe akulu akulu ao ankalankhula anali ndi mphamvu kwa iwo kuposa Mau a Mulungu. Choncho, ngakhale nthawi imene Yesu anali mdziko lino, anthu anakhulupilira ndi kulemekeza kwambiri mau a akulu akulu ndi kukhala molingana ndi mauwo, monga kunalembedwa, “Pakuti Afarisi, ndi Ayuda onse sakudya osasamba m’manja ao, kuti asungire mwambo wa akuru”(Marko 7:3). Choncho, Yesu anati kusakhulupilira Mau amene Iye analankhula ndi kuwataya, kusadziwa mu mtima Mau a Yesu monga Mau a Mulungu, ndi tchimo lalikuru. 

Tiyenera kudziwa cholinga cha lamulo. Mwanjira ina, tiyenera kudziwa chifukwa chimene Mulungu anatipatsila malamulo 613 omwe muli “chitani komanso musachite” mwa ndondomeko. Choyamba Mau a lamulo omwe Mulungu analankhula yekha ndi choondi ndipo Iye anapatsa Mau pofuna kukhadzikitsa njira ya choonadi, ndipo Mau anakhala lamulo lomwe Mulungu analankhula ku mtundu wa anthu. Anthu anabwera kulandira chipulumutso ku machimo posiyanitsa choonadi ku chabodza mwa Mau a lamulo lomwe Mulungu analankhula ndi kulandira chipulumutso ku machimo pokhulupilira mu choonadi. Chachiwiri, Ambuye ananena kuti ndi chabwino kukhulupilira mu Mau omwe Yesu analankhula ndi kukhala molingana ndi Mauwo ngati anthu a Mulungu. Choncho, tiyenera kukhala mwa chikhulupiliro. Koma, tonse aife amene tikhulupilira mwa Mulungu takhala ochimwa pamaso pake chifukwa sitikanakhala molingana ndi Mau olembedwa a Mulungu, ndipo motero kunali koyenera kuti ife tilandire chipulumutso pokhulupilira mu Mau a Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu omwe Mulungu anakwaniritsa potuma Yesu kwa ife. 

Komabe anthu anakhala kutali ndi Mulungu ndipo anayandikana ndi mdierekezi chifukwa sadziwa Mau omwe Yesu analankhula ndipo m’malo mwake anawanyoza Mauwo. Choncho, kusakhulupilira m’Mau a Yesu kukupanga tchimo lalikulu kwa anthu. Ngakhale kusasunga Mau a Mulungu komanso zolakwa ndi machimo, kusakhulupilira m’Mau a Mulungu koma m’malo mwake kuwakana ndi tchimo lalikulu lolimbana ndi Mulungu lomwe limapangitsa munthu kuyenera kudana ndi Mulungu, ndipo anthu onse otere akuyenera gahena chifukwa cha tchimo losakhulupilira m’Mau ake. Tchino la chinyengo komanso loyenera gahena pamaso pa Mulungu ndi tchimo lokana Mau a Mulungu ndi kusakhulupilira mwa iwo.

Kodi mukuganiza kuti cholinga cha lamulo limene Mulungu anapatsa mtundu wa anthu ndi chiani? Ndikupanga anthu kuzindikira machimo ao onse ndi kupanga iwo kubwerera kwa Mulungu. Chinali chifuniro cha Mulungu kuti lamulo lipange anthu amene anachoka kwa Mulungu chifukwa sanakhulupilire m’Mau kubwerera kwa Mulungu, komanso malamulo a zoyenera kuchita ndi zosayenera kuchita zomwe zikuoneka mu lamulo zakhala amphunzitsi omwe atsogolera ochimwa kwa Yesu (Agalatiya 3:24-25). Mulungu anapatsa malamulo 613 pofuna kupanga anthu onse kuzindikira machimo ao mwa lamulo ndi kubwerera kwa Mulungu ndi kukhala olungama polandira chikhululukiro cha machimo kudzera muchikhupiliro chokhulupilira mwa Yesu.

Obadwa-mwatsopano oyera mtima amadziwa bwino chifukwa chimene Mulungu anaperekera lamulo kwa anthu chifukwa Buku la Aroma 3:20 akunena kuti Mulungu anapatsa lamulo kuti apange anthu kuzindikira uchimo. Nanga, kodi tikuzindikira chiani kudzera mu lamulo la Mulungu? Lamulo limatipangitsa ife kuzindikira kufooka kwa munthu; timazindikira kudzera mu lamulo kuti nzosatheka kuti ife tisunge malamulo a Mulungu, lamulo. 

Kodi timazindikira chiani kudzera mu mumalamulo 613 a Mulungu? Timazindikira kakhalidwe ka tchimo la anthu. Timazindikiranso zoona zeni zeni za Mulungu. Timazindikira zolakwa za zochitika za munthu, za omwe sangasunge ndikutsata Mau a Mulungu, komanso kulephera kwa thupi la munthu. Mwachidule, timazindikira kuti ife tonse tikuyenera ku gahena chifukwa cha machimo athu. Nanga, kodi tiyenera kuchita chiani tikazindikira kulephera kwathu komanso machimo? Kodi munthu ayenera kuyesa molimba kusintha kulephera kwake mwa chikhulupiliro pokhulupilira mu chikhulupiliro cha ngwiro posachedwapa? Ai, iye asatero. M’malo mwake choyamba iye ayenera kudziwa kulephera kwake. Kenako ayenera kulandira chipulumutso pokhulupilira mu Uthenga Wabwino oyamba wa madzi ndi mwazi wa Yesu amene ndi mpulumutsi ndi kuthokoza Iye. Anthu amene amakhulupilira m’Mau a madzi ndi Mzimu ayenera kuzindikira kuti Mulungu anapanga anthu kuzindikira kuti iwo ndi ochimwadi ndi kupanga iwo kulandira chipulumutso chimene Yesu Kristu anapulumutsira iwo ku machimo ao onse adziko, ku gahena, mwa madzi ndi mwazi.

Cholinga chimene Mulungu anaperekera lamulo kwa anthu chinali kuwaphunzitsa iwo kuzindikira kotheratu kuti ndi ochimwa. Ndipo ife tiyenera kudziwa kuti Mulungu anatuma Mwana Wake Yesu kutipatsa ife chikhululukiro cha machimo athu onse popanga Yesu kutenga machimo a mtundu wa anthu onse pa Iye Yekha kudzera mu ubatizo omwe analandira. Monga chonchi, Mulungu anatipatsa lamulo kuti atipange ife kukhala ana ake kudzera mu chipulumutso chake cha machimo athu onse mwa Yesu Kristu. Mulungu anatipatsa lamulo la Mulungu kwa ife omwe ndife mbeu ya Adamu pofuna kutipanga inu ndi ine ana ake. Tiyenera kuzindikira kuti tchimo ndi chiani komanso kudziwa kuti ndife ochimwa a chinyengo otheratu ndi kukhala ana a Mulungu omasulidwa ku uchimo pokhulupilira mu ubatizo wa Yesu omwe analandira komanso mwazi omwe anakhetsa. Ndipo tiyenera kukhala moyo obwezera ulemelero kwa Mulungu.

Tiyenera kuganiza za Mau a malembo monga Mau a Mulungu ndi kukhulupilira m’Mauwo monga Mau a Mulungu. Koma ngati sichoncho, ngati tikhulupilira Mau a Mulungu ndi maganizo athu osokonekera oipa amene amachoka mwa ife, tidzagwera mu zolakwika komanso kugwera ku chionongeko. Choncho, tiyenera kuphunzira ndi kukhulupilira m’Mau olembedwa a Mulungu ogona pa Mau a madzi ndi Mzimu. Abale ndi alongo, ngakhale a Israyeli, Afarisi komanso Alembi, sakanadzudzula ophunzira a Yesu pokudya mkate osasamba m’manja akanakhala kuti anaona mu kuunika kwa Mau a Mulungu. Ndi chifukwa Ambuye anati munthu anadetsedwa ndi machimo khumi ndi awiri amene ali m’kati mwa munthu.

Kodi ndi machimo otani omwe ali mkati mwa munthu? Mu Uthenga Wabwino wa Marko 7:21-23, Ambuye akuti anthu amakhala onyansa chifukwa cha mitundu khumi ndi iwiri ya machimo, monga kunalembedwa, “Pakuti m’kati mwace mwa mitima ya anthu, muturuka maganizo oipa, zaciwerewere, zakuba, zakupha, zacigololo, masiriro, zoipa, cinyengo, cinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa: zoipa izi zonse zituruka m’kati nizidetsa munthu.” Iye ananena kuti anthu ali ndi mitundu khumi ndi iwiri ya machimowa mwachibadwidwe omwe amawapanga iwo, anthu ena, komanso dziko lonse kunyansa.

Kunalembedwa m’Buku la Masalmo 8:3-4, “Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, nchito ya zala zanu, Mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika, munthu ndani kuti mumkumbukila? Ndi mwana wa munthu kuti muceza naye?”

N’chifukwa chiani Mulungu akulimbikitsa anthu kuti abadwe mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu? Akunena kuti Mulungu akulimbikitsa anthu chifukwa Iye amawakonda. Ndipo Ambuye analenga anthu ndi kuwamvera chisoni iwo ndi kuwakonda iwo osagwirizana ndi chikondi cha Mulungu komanso chipulumutso cha madzi ndi Mzimu, ndipo potero kufafaniza machimo onse a anthu osayenera ndi kupulumutsa iwo. Ndipo iwo anati adzawapanga iwo kukhala anthu ake eni eni. Kunalembedwa mu Masalmo, “Yehova, Ambuye wathu, dzina lanu liposadi nanga padziko lonse lapansi!” (Masalmo 8:1). Ili ndi salmo lomwe olemba wa Buku la Masalmo analemba atazindikira kuti Yesu ndi mpulumutsi amene anamupulutsa iye ku machimo ake onse. Ndipo mtumwi Paulo analankhula za chikhulupiliro chomwechi m’Chipangano Chatsopano. Iye akunena kuti chipulumutso ndi chachikulu ndiponso ntchito yodabwitsa kwambiri pantchito zomwe Mulungu anachita kwa ife, ndipo cholengedwa chafika pa umulungu omwe unakhazikitsidwa ngati choonadi chifukwa cha chifundo cha Mulungu.

Tiyenera kukhulupilira m’Mau onse odalitsika a Yesu. Chipulumutso cha madzi ndi Mzimu ndi magalasi a chikondi cha Mulungu kwa anthu. Ambuye anatiphunzitsa ife kuti ndi kupusa kuyesera kusunga lamulo ngakhale tili opelewera ndipo maganizo otere amachokera m’kati mwa umbuli wa munthu. Choncho tiyenera kumvetsetsa kuti ndi zachabe chabe kuyesera molimba kuthana ndi tchimo pamene tili pansi pa lamulo. Mulungu akufuna anthu monga ife amene tili achinyengo ndi ochimo akuyenera ku gahena kuti tibwere ndikuzindikira kuti uchimo ndi chiani kudzera mwa lamulo ndi kubadwa mwatsopano pokhulupilira m’Mau a Uthenga Wabwino wa choonadi omwe Yesu anapulumutsa ife pobwera mwa madzi ndi mwazi ndi Mzimu.Anthu mwachibadwidwe anabadwa monga mulu wa uchimo ndipo mitima yao inadetsedwa ndi machimo amene amachita moyo wao onse


Yesu ananene kuti machimo amene amaturuka mu mtima mwa munthu amadetsa munthu. Ambuye ananena kuti zakudya zonse siziipitsa munthu, koma mitundu khumi ndi iwiri ya machimo yomwe imachoka mwa munthu ndi yomwe imaiipitsa munthu. Timachimwa chifukwa tinabadwa ndi mitundu yosiyana siyana ya machimo monga mbeu ya Adamu. Ngati munthu amene anabadwa ndi uchimo wadziwa cholinga cha lamulo la Mulungu, ayenera kuleka kuyesera kusunga lamulo la Mulungu ndi mphamvu zake ndi kukhulupilra m’Mau a choonadi akubadwa mwatsopano. Ngati munthu akufuna kulandira chikhululukiro cha machimo, ayenera kukhulupilira kuti Yesu anabatizidwa kuti achotse machimo onse adziko, ndipo Iye anakhetsa mwazi kuti atetezere machimo onseo, ndipo kuti Yesu ndi Mulungu Yekha komanso Mwana wa Mulungu Atate, mpulumutsi wa anthu onse. 

Malamulo onse a Mulungu ndi olungama koma anthu ndi mulu wa uchimo chifukwa cha tchimo lomwe anatenga poti anabadwa m’mimba za amayi awo. Pamene tikuyang’ana pa mitundu khumi ndi iwiri ya machimo yomwe ndi yosemphana ndi malamulo a Mulungu, tingathe kumvetsetsa kuti ndife anthu amene tiyenera kulandira chifundo ndi chipulumutso kwa Mulungu. Ochimwa amabwera kufuna chipulumutso cha chikhululukiro cha machimo chomwe chimaperekedwa mwa Mau okha a madzi ndi Mzimu a Yesu.

Tingathe kuona Davide kudzera m’Mau a malembo mu Masalmo 51:4. Davide anabvomereza, “Pa Inu, Inu nokha, ndinacimwa, ndipo ndinacicita coipaco pamaso panu: kuti mukhale olungama pakulankhula Inu, mukhalenso woyera pa kuweruza kwanu.” Izi zikutanthauza kuti Davide anaziwa kotheratu kuti anali mulu wa uchimo ndipo kuti iye anali ochimwa ngati Ambuye ananena kuti anali ochimwa ndiponso kuti iye anali olungama ngati Ambuye ananena kuti anali olungama, ndipo kuti iye angalandire chipulumutso ngati Mulungu wampulumutsa iye ndipo kuti iye angapite ku gahena ngati Mulungu wamponya ku gahena. Chikhulupiliro chotere ndi chikhulupiliro choongoka ndipo mtima wa malingaliro otere ungalandire chikhululukiro cha machimo onse. 

Chifukwa anthu onse ndi mbeu ya Adamu, tili ndi zonyansa m’kati mwa mitima yathu, mtima wakupha m’kati mwa mtima, mtima osalemekeza makolo, komanso machimo ena kupatula machimo amenewa. Choonadi chimene tiyenera kumvetsetsa apa n’chakuti Mau onse a Mulungu ndi olungama moonadi ndipo kuti tizindikire kuti ife anthu ndife mulu oipa wa uchimo. Koma, kodi anthu amadziwa Mau a Mulungu? Lingaliro lonena kuti, “sindinali ochimwa dzulo chifukwa ndinachita tchinto zabwino, koma ndine ochimwa lelo chifukwa ndachita chintu choipa,” izi si zoona, koma ndi maganizo chabe a umunthu. Choncho kunali bwino kuti munthu akhale ndi mtima wa malingaliro olemekeza Mau a choonadi onena kuti munthu sangakwanitse koma kupita ku gahena chifukwa ndi mulu wa machimo otheratu kuchoka tsiku lobadwa pamaso pa Mulungu ngakhale iye sanaphwanyepo lamulo la Mulungu. Munthu amene amabvomereza Mau a choonadi omwe Mulungu analankhula ngati awa ndi munthu amene wazidziwa yekha ngati mulu wa uchimo.

Anthu ndi mbeu yakuchita zoipa osati chifukwa akuchita chigololo, akupha, akuba komanso sangakonde anthu ena, koma chifukwa iwo anabadwa monga mulu wa machimo pa chiyambi kuchoka patsiku la kubadwa; sangakwanitse koma kupita ku gahena chifukwa anabadwa ndi chilengedwe cha uchimo chomwe ndi chosemphana ndi chiyero; ndipo, choncho, ayenera kubvomereza kuti ali mulu wa uchimo ndi kuzindikira ndi kukhulupilira m’Mau a Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu omwe Ambuye anapereka chifukwa sangakwanitse kuchita ntchito ili yonse yolungama.

Kodi munthu amene anabadwa ndi mtima wa kupha angakhale olungama opanda tchimo pamaso pa Mulungu chifukwa chakuti sanachite tchimo? Anthu ndi ochimwa mwachibadwidwe, mulu wa uchimo, onyenga, komanso osalungama omwe ayenera ku gahena. Yesu anauza Afarisi ndi Alembi kuti sangazembe chiweruzo cha ku gahena, ponena kuti, “tsoka kwa inu Alembi ndi Afarisi, onyenga!” anthu sangakwanitse koma kuchimwa moyo wao onse chifukwa anabadwa ngati milu ya uchimo. Kodi mumachita tchimo moyo wanu onse? Kodi izi ndi zoona? Ngati izi ndi zoona, khulupilirani mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo. Ndi kufuna inu mukhulupilire mu Uthengawu ndi kulandira chipulumutso. Mulungu akhale nanu nthawi zonse!