Sermons

【3-11】< Eksodo 12:43-49 > Kodi Uthenga Wabwino Unakwaniritsidwa ndi Mwazi Okha, kapena ndi Madzi, kapena ndi Zonse?< Eksodo 12:43-49 >

“Ndipo Yehova anati kwa Mose ndi Aroni, lembani la Paskha ndi ili: mwana wa mlembo ali yense asadyeko; koma kapolo wa mwini ali yense, wogula ndi ndarama, utamdula, ndipo adyeko. Mlembo kapena wolembedwa nchito asadyeko. Audye m’nyumba imodzi; usaturukira nayo kubwalo nyama yina; ndipo musathyole pfupa lace. Msonkhano wonse wa Israyeli uzicita ici. Koma akhale nanu mlendo, nakonzera Yehova Paskha, adulidwe amuna ace onse, ndipo pamenepo asendere kuucita; nakhale ngati wobadwa m’dziko; koma wosadulidwa ali yense asadyeko. Pakhale lamulo lomweli pa wobadwa m’dziko, ndi pa mlendo wakukhala pakati pa inu.”Zonse Chipangano Chakale ndi Chipangano Chatsopano ndi zofunika komanso zamtengo wapatali kwa ife, amene takhulupilira mwa Mulungu. Sitinganyalanyaze ngakhale liwu limodzi la m’Chipangano Chakale. Izi ziri chonchi chifukwa Mau onse a Ambuye ndi Mau a moyo. Ndipo Ambuye anati, “Thambo ndi dziko lapansi zidzacoka, koma mau anga sadzacoka ai” (Mateyu 24:35).

Ndime ya malembo a lero ikutiuza ife kuti ali yense amene akufuna kusunga Paskha choyamba ayenera kudulidwa. Mwanjira ina, osadulidwa, sangakudzidwe mu chikondwerero cha Paskha. Tiyenera kuganiza chimene Mulungu anatipatsira lemba lotere.

Tiyenera kumvetsetsa cholinga cha Ambuye kumbuyo kwa lemba lokhudza mdulidwe. Mdulidwe ndi mwambo omwe amadula khungu la nsonga la maliseche. Kodi n’chifukwa chiani Mulungu anauza Abrahamu ndi mbeu yake kuti adulidwe? Linali longjezo la Mulungu kuti Iye adzatenga anthu odulidwa, anthu omwe machimo ao anadulidwa, kukhala anthu Ake. Pachifukwa icho, Mulungu anauza Israyeli kuti adulidwe. A Israyeli anayenera kudulidwa kuti akhale anthu a Mulungu. Mdulidwe unali lamulo la Mulungu. Mulungu anakhala Mulungu wa iwo amene machimo ao anadulidwa podulidwa mu mtima mwa chikhulupiliro. Ngakhale m’Chipangano Chatsopano, Mulungu ndi Mulungu wa iwo amene machimo ao anadulidwa mwa chikhulupiliro.Kodi Paskha ndi Chiani?


Tchuthi chachikulu cha a Israyeli chinali Paskha. Chikondwelero cha zokolola chinalinso tchuthi chofunika chotsatira. Koma, ku Israyeli Paskha chinali tchuthi chofunika kwambiri. Izi ziri chonchi chifukwa Mulungu anawachotsa iwo ku Aigupto patatha zaka 430 za ukapolo. Pamene Mulungu anachotsa a Israyeli ku Aigupto, anakhotetsa mtima wa Farao kudzera matsoka khumi ndi kutsogolera Israyeli mu mzinda wa kanani. Israyeli anapulumutsidwa ku tsoka lotsiriza, imfa ya mwana wamwamuna oyamba, mwa mwazi wa mwanawankhosa wa Paskha. Pa chifukwa ichi Mulungu anati kwa Israyeli, “sungani Paskha.”Kodi tingadye bwanji chikondwerero cha paskha

 

Tiyenera kuti mdulidwe ndi chibvomerezo cha ali yense amene akufuna kudya chikondwelero cha Paskha. Ngati wina sanadulidwe, sankatenga mbali mu chikondwelero cha Paskha. Kuti Israyeli asunge Paskha ankayenera kuchita chinthu chimodzi Paskha isanachitike, ndipo chinali kudulidwa. Ndime ya lero ikutiuza ife kuti tidulidwe kuti tisunge Paskha; “Ndipo Yehova anati kwa Mose ndi Aroni, lembani la Paskha ndi ili: mwana wa mlembo ali yense asadyeko; koma kapolo wa mwini ali yense, wogula ndi ndarama, utamdula, ndipo adyeko. Mlembo kapena wolembedwa nchito asadyeko. Audye m’nyumba imodzi; usaturukira nayo kubwalo nyama yina; ndipo musathyole pfupa lace. Msonkhano wonse wa Israyeli uzicita ici. Koma akhale nanu mlendo, nakonzera Yehova Paskha, adulidwe amuna ace onse, ndipo pamenepo asendere kuucita; nakhale ngati wobadwa m’dziko; koma wosadulidwa ali yense asadyeko. Pakhale lamulo lomweli pa wobadwa m’dziko, ndi pa mlendo wakukhala pakati pa inu.” (Ekisodo 12:43-49). 

Ndani amene ankayenera kudya Mwanawankhosa amene ankaperekedwa pa Paskha? Mwanjira ina, ndani akanasunga Paskha? Okhao amene anadulidwa pakati  pa Israyeli ali ndi mwayi osunga Paskha. Monga mukudziwa, Mwanawankhosa operekedwa pa Paskha ndi Yesu, amene anachotsa machimo adziko lapansi.

Nanga kodi mdulidwe wa m’Chipangano Chakale ukutanthauza chiani m’Chipangano Chatsopano? Mdulidwe ukutanthaunza kudula nsonga  ya kutsogolo kwa maliseche a mwamuna. Yesu nayenso anadulidwa masiku asanu ndi atatu pamene Iye anabadwa. Popeza Mulungu anati iwo ayenera kudulidwa poyamba, ndipo ali yense osadulidwa sankasunga Paskha, mdulidwe sunali chisanko; amayenera kuchita zomwe Mulungu wanena. Ngati mukuganiza kuti mu makhulupilira mwa Yesu, muyenera kumvetsetsa kuti mdulidwe ndi chiani m’Chipangano Chatsopano.Kodi Mwambo wa Mdulidwe umene Mulungu analamula Abrahamu Kuchita unali Otani?


Pamene tikuyang’ana m’Buku la Genesis, tikuona kuti Mulungu anapanga pangano kwa Abrahamu ndi mbeu yake kuti adulidwe. Mu Genesis 15, Mulungu analojeza Abrahamu kuti adzamupatsa iye mzinda wa Kanani komanso mu mbeu yake yambiri monga nyenyezi kumwamba; ndipo mu 17, Mulungu anauza Abrahamu kuti iye ndi mbeu yake ayenera kudulidwa ngati chikole kwa Mulungu ngati akufuna kukhala anthu a Mulungu. Mulungu anati mdulidwe mu thupi ndi chiziwitso choti akhala anthu a Mulungu ndipo Iye adzakhala Mulungu wao. Mu Genesis 17:7-8, Mulungu analamula Abrahamu ndi mbeu yake kuti adulidwe monga chidziwitso chapangano; “Ndipo ndidzalimbitsa pangano langa ndi Ine ndi iwe pa mbeu zako za pambuyo pako m’mibadwo yao, kuti likhale pangano la nthawi zonse, kuti ndikhale Mulungu wako ndi wa mbeu zako za pambuyo pako. Ndipo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako, dziko la maulendo anu, dziko lonse la kanani likhale lako nthawi zonse: ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao.” Kodi Mdulidwe wa Uzimu ndi Chiani?


Abrahamu anakhulupilira lonjezo la Mulungu, ndipo Mulungu anamuyesa iye olungama. Kodi chidziwitso cha pangano la Mulungu limene anapanga ndi Abrahamu komanso mbeu yake chinali chotani? chinali mdulidwe. “Ili ndi pangano limene uzisunga pakati pa Ine ndi iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako: azidulidwa amuna onse a mwa inu” (Genesis 17:10). 

Mdulidwe ndi kudula kwa nsonga ya maliseche, ndipo ukuimilira kupereka kwa uchimo pa Yesu pokhulupilira mu madzi a ubatizo wa Yesu mtsinje wa Yordano. Mwauzimu, kunali kudula machimo ao polandira madzi a ubatizo wa Yesu; ndipo unali mdulidwe wa chipulumutso chakale. Ukutanthauza mdulidwe wa chikhululukiro cha machimo, umene unakwaniritsidwa mwa ubatizo wa Yesu mu mtsinje wa Yordano.

Mdulidwe m’Chipano Chakale unali chithunzi thunzi cha ubatizo wa Yesu m’Chipangano Chatsopano, ndiponso pangano la anthu m’Chipangano Chakale ndi chatsopano kuti akhale anthu a Mulungu. Mwa chidule, mdulidwe  m’Chipano Chakale unali ubatizo wa Yesu m’Chipangano Chatsopano. Monga m’mene machimo adziko anapatsidwira pa Yesu pamene Yohane Mbatizi anambatiza Yesu m’njira yoika manja, mbeu ya Abrahamu inalindira chidziwitso cha pangano kuti ikhale anthu Mulungu kudzera mu mdulidwe omwe unadula nsonga ya maliseche ao.

Ubatizo wa Yesu unadula machimo kwa ochimwa ndi kupanga ochimwa kukhala oyera. Monga m’mene ankadulira nsonga, machimo anaperekedwa kwa Yesu pamene Iye anabatizidwa; ndipo ali yense wakhulupilira mu choonadi choti Yesu anathana ndi mabvuto onse a uchimo pamene Yohane Mbatizi anaika manja ake pamutu pa Yesu anadulidwa mwa uzimu ndi kukhala m’modzi mwa anthu olungama a Mulungu.Chikhulupiliro Chimene Chimapangitsa Munthu Kulekana ndi Mulungu


Mulungu anati adzalekanitsa osadulidwa ku a Israyeli. Ndiyeno kodi mdulidwe ndi chiani? Kodi izi zikutanthauza chiani mu uzimu? Mdulidwe wa kuthupi ndi kudula khungu la nsonga pamene mudulidwe wa uzimu wa Uthenga Wabwino wakale unali kupatsila machimo onse amtundu onse wa anthu pa Yesu. Ubatizo wa Yohane Mbatizi omwe anapatsa Yesu unali mdulidwe wa uzimu omwe unadula machimo onse a dziko ndi kuika machimowo pa thupi la Yesu. Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi kuti machimo onse a mtundu onse wa anthu achotsedwe.

Machimo onse a mtundu onse wa anthu anaikidwa pa Yesu. Mulungu anapangana pangano ndi Abrahamu komanso mbeu yake ndipo anapanga iwo kudulidwa ndi cholinga choti Iye akhale Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, Mulungu wa Yakobo komanso Mulungu wa mbeu zao. Ndi Iye anakhala Mulungu wa iwo amene machimo ao anadulidwa mwa mdulidwe.

Mdulidwe omwe umadula machimo unali lonjezo la Mulungu lomwe Iye anapangana ndi Abrahamu komanso anthu amene akhulupilira mu Ubatizo ndi mwazi wa Yesu monga chipulumutso chao. Mulungu anali Mulungu wa iwo amene anadulidwa. Ichi ndi chifukwa chake, pamene a Israyeli anachoka ku Aigupto, Mulungu anauza Mose za pangano la mdulidwe:

“Muzidula khungu lanu; ndipo cidzakhala cizindikiro ca pangano pakati pa Ine ndi inu. A masiku asanu ndi atatu azidulidwa mwa inu, ana amuna onse a m’mibadwo mwanu, amene abadwa m’nyumba ndi amene agulidwa ndi ndalama kwa alendo ali onse, wosakhala mwa mbeu zako Azidulidwatu amene abadwa m’nyumba mwako ndi amene agulidwa ndi ndalama zako: ndipo pangano langa lidzakhala m’thupi mwako pangano losatha. Ndipo mwamuna wosadulidwa khungu lace, munthuyo amsadze mwa athu a mtundu wace; waphwanya pangano langa (Genesis 17:12-14).

Iwo amene amayesa kukhulupilira mwa yesu popanda mdulidwe wa uzimu amachotsedwa pakati pa anthu a Mulungu, pakuti mdulidwe wa uzimu unali ubatizo wa Yesu ndi Yohane Mbatizi kuti achotse machimo onse a adziko lapansi. Iwo amene akhulupilira mwa Yesu ayeneranso kubvomera mdulidwe m’Chipangano Chakale komanso ubatizo wa uzimu mwa Yesu pofuna kuti alandire chipulumutso ku machimo ao onse komanso kuti alandire Mzimu Woyera kuti akhale anthu a Mulungu. Kwa iwo amene amakhulupilira mwa Yesu, mdulidwe m’Chipangano Chakale ndi ubatizo wa Yesu m’Chipangano Chatsopano ndi zinthu zofanana.

Ngati sitimvetsetsa tanthauzo leni leni la mdulidwe kapena mdulidwe wa uzimu omwe umabweretsa chipulumutso cheni cheni, tikukhulupilira mwa Yesu mwachabe; ngati tikuganiza kuti tili ndi chikhulupiliro cholimba, tikumanga nyumba ya chikhulupiliro pamchenga. Mulungu anauza anthu ake kuti adulidwe. Izi zikutanthauza kuti Iye akufuna m’Kristu ali yense kukhulupilira mdulidwe wa uzimu, ubatizo wa Yesu omwe unatsuka machimo adziko lonse. Popanda chidziwitso cha mdulidwe mu thupi, sindife anthu a Mulungu. Osadulidwa ankachotsedwa pakati pa anthu a Mulungu. Pachifukwa icho, Mulungu analamula a Israyeli kuti onse alendo ndi akapolo ayenera ku dulidwa asanasunge Paskha. Mulungu anachenjeza kuti adzachotsedwa kwa Mulungu ngati iwo sanadulidwe. Lemba limeneli lomwe Mulungu anaika pa  Israyeli likutanthauzanso kwa ali yense amene amakhulupilira mwa Yesu. 

Eksodo 12 akutiuza ife kuti a Israyeli ayenera kudulidwa asanadye Mwanawankhosa ndi ndiwo zowawa zomwe ankaloledwa iwo kudya pa phwando la Paskha. Tonse tiyenera kumvetsetsa kuti iwo a Israyeli amene ankadya Mwanawankhosa ndi kupaka mwazi wake pa mphuthu za mbali ndi pamwamba pa nyumba zao anali adadulidwa kale. Choncho, ali yense amene watenga mbali pa chikondwelero cha Paskha ankayenera kudulidwa. Linali pangano la Mulungu kuti anthu osadulidwa ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu a Mulungu. Mulingaliro la uzimu, ndi tchimo lopereka ku chionongeko chifukwa chosowa chikhulupiliro.  Choncho, tiyenera kuzindikira kuti mdulidwe wa muzimu pali njira yokhayo yolandilira chipulumutso kwa Ambuye.Kodi Mdulidwe Umene ali Yense Ayenera Kuyang’anapo ndi Chiani?


Tsopano pali china chake chimene tiyenera kukambilana. Tiyenera kukumbukira kuti a Israyeli ankadulidwa asanatenge mbali muchikondwelero cha Paskha. Abrahamu ndi mbeu yake anakhala anthu a Mulungu podulidwa. M’Chipangano Chakale iwo amene sanadulidwe sakanakhala anthu a Mulungu; anataya ufulu otenga mbali pa phwando la Paskha. Okhao amene anaika chikhulupiliro chao mu pangano ndipo anadulidwa ndi omwe akanakhala ana a Mulungu.

Okhulupilira a Yesu ayenera kulandira mdulidwe wa uzimu omwe umabweretsa chikhululukiro cha machimo komanso kukhala nzika ku ufumu wa Mulungu. Israyeli, amene anadulidwa mu thupi, anakhala pamodzi mu Aigupto kwa zaka zokwana 430 pansi pa ukapolo owawa mwa kupereka kwa Mulungu. Iwo ankapemphera kwa Mulungu,  “oh, Mulungu chonde tichotseni ife ku Aigupto.” Mulungu anayankha mapemphero ao. Iwo akanachoka ku Aigupto popaka mwazi wa Mwanawankhosa pa mphuthu za mbali ndi ya pamwamba m’nyumba zimene ankakhalamo. Pamene ankafuna kusunga Paskha mu chipululu, osadulidwa amayenera kudulidwa mu thupi asanatenge mbali pa phwandolo. Israyeli anapha Mwanawankhosa ndi kupaka mwazi wake pa mphuthu za mbali ndi ya pamwamba pamene m’ngelo wa imfa ankadutsa m’nyumba zawo. Chifukwa cha ichi imfa sinalowe m’makomo mwao koma m’malo mwake inawapitirira; imfa sinagwere pa iwo, koma tsokali linawapitirira iwo.

Kuchoka pa nthawi ya Abrahamu, anthu Israyeli ankadulidwa pamene anali ndi masiku asanu ndi atatu akubadwa. Israyeli amene anakhala anthu a Mulungu ankaopa Mulungu ndi kulilira Mulungu kuti awapulumutse kuzowawa zao. Anthu Israyeli amene anakhala mu Aigupto amayenerabe ku dulidwa ndipo okhao amene anadulidwa pamene anakwana masiku asanu ndi atatu akubadwa anazindikiridwa ngati anthu a Mulungu. Ichi ndi chimodzi modzi ndi mdulidwe wa machimo mu nthawi ya Yesu pokhulupilira mu ubatizo wa Yesu. Iwo analandira mdulidwe mu thupi chifukwa anakhulupilira mu zomwe Mulungu analonjeza Abrahamu.

Patatha zaka mazana, Mulungu anapanga pangano lomweli la mdulidwe wa mu thupi ndiye anthu amene ankapita ku mzinda wa Kanani. Eksodo 12:47-51 akuti, “Msonkhano wonse wa Israyeli uzicita ici. Koma akakhala nanu mlendo, nakonzera Yehova Paskha, adulidwe amuna ace onse, ndipo pamenepo asendere kuucita; nakhale ngati wobadwa m’dziko; koma wosandulidwa ali yense asadyeko. Pakhale lamulo lomweli pa wobadwa m’dziko, ndi pa mlendo wakukhala pakati pa inu. Ndipo ana onse a  Israyeli anacita monga Yehova adawalamulira Mose ndi Aroni, momwemo anachita. Ndipo kunakhala tsiku lomwelo, kuti Yehova anaturutsa ana a Israyeli m’dziko la Aigupto, monga mwa makamu ao” linali lamulo la Mulungu kuti ali yense amene adzasunga Paskha ayenera kudulidwa, komanso ali yense amene watenga mbali mu Paskha popanda kudulidwa achotsedwe pakati pa anthu.

 Mulungu akutiuza ife kuti tikhulupilire kuti mdulidwe wa thupi m’Chipangano Chakale unali mdulidwe wa uzimu omwe Yesu anachita kuti adule machimo kwa ochimwa.

1 Petro 3:21 ikuti, “Cimenenso cifaniziro cace cikupumutsani tsopano, ndico ubatizo, kosati kutaya kwa litsoro lace la thupi, komatu funso lace la cikumbu mtima cokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Kristu.” Ndi kufunsa inu amene mumakhulupilira mwa Yesu: “kodi mumakhulupilira zoona zakuti machimo anu onse anatengedwa ndi kuperekedwa kwa Yesu kudzera mu ubatizo wake?” Ngati mukumvetsetsa ndi kukhulupilira zoona za ubatizo mwazi wa Yesu, mwazindikira kuti mwakhala oyera mtima amene adulidwa mu uzimu. Ndipo mudzakhulupilira chilungamo cha uzimu chimene popanda ubatizo wa Yesu sipangakhale nsembe ya mwazi wake pamtanda. Ngati mumakhulupilira mu mtanda okha ndipo osati mu ubatizo wa Yesu, omwe umapereka chikhululukiro cha machimo, mudzazipeza nokha kutali ndi chifundo cha Mulungu ndi kukhalabe mu uchimo. 

Mdulidwe m’Chipangano Chakale unali kudula khungu la nsonga la munthu, koma mdulidwe wa uzimu umapezeka mwa chikhulupiliro chokhulupilira kuti ubatizo wa Yesu unachotsa machimo athu onse ndi kubweretsa chipulumutso kwa ife. Tiyenera kukhulupilira chilungamo choti chipulumutso cha machimo chimayamba kuchokera ku ubatizo wa Yesu ndi kuthera ku mwazi wa Yesu. Pobvomereza ndi kukhulupilira mau a ubatizo ndi mwazi wa Yesu tingakhale ana akuunika. Chikhulupiliro chotere chimasiyanitsa anthu obadwa mwatsopano ku anthu omwe sanabadwe mwatsopano.

Ambuye wathu anachotsa machimo adziko ndi ubatizo wake ndi mwazi wake, ndipo akutiuza ife kuti tikhulupilire mwa Iye. Choncho, ngati tikufuna kukhala ndi umboni wa Mulungu kuti tinakhala anthu a Mulungu, tiyenera kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu. Ngati si choncho,  tidzachotsedwa kwa Yesu. Mdulidwe wa uzimu wa chipulumutso cha machimo ndi ubatizo wa Yesu, ndipo mdulidwe wa m’Chipangano Chakale ndi chikhulupiliro chodula khungu la munthu. Chipulumutso chimakwaniritsidwa mwa chikhulupiliro mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi wa Yesu, Mwanawankhosa wa Paskha. Chifaniziro cha mdulidwe wa thupi m’Chipangano Chakale ndi ubatizo wa Yesu m’Chipangano Chatsopano. Yesaya 34:16 akunena kuti Mau a Mulungu ali ndi anzake a iwo: “Funani inu m’buku la Yehova, nimuwerenge; kulibe umodzi wa iye udzasowa, palibe umodzi udzasowa unzace; pakuti pakamwa pa Yehova panena, ndipo Mzimu wace wasonkhanitsa iwo.”  Mau a m’Chipangano Chakale ali ndi anzake m’Chipangano Chatsopano. Palibe ndime ngakhale imodzi yomwe ingasowe inzake. Ndiyeno ndi ndime Iti m’Chipangano Chatsopano yomwe ndi inzake ya mdulidwe wa thupi m’Chipangano Chakale? Ndi ubatizo wa Yesu mu mtsinje wa Yordano omwe unachotsa machimo onse adziko. Mdulidwe wa chipulumutso cha myoyo yathu ndi ubatizo wa Yesu m’Chipangano Chatsopano (Mateyo 3:13-17). Ndani Amakhulupilira Mopusa Mamphunziro Olakwika?


Masiku ano anthu ambiri amangokhulupilira mu mwazi wa Mwanawankhosa wa Paskha. Iwo amaganiza, “kodi mdulidwe n’chiani? Unali wa Ayuda m’Chipangano Chakale. Kodi mdulidwe omwe tikufunika kulandira mu nthawi ya Chipangano Chatsopano?” Izi zikumveka ngati zoona, koma sindikukamba za mdulidwe wa thupi; ndikunena za mdulidwe wa uzimu omwe mtumwi Paulo anakambapo m’Chipangano Chatsopano. Akristu ambiri amakana mdulidwe wa uzimu omwe umabweretsa chikhululukiro cha machimo. Mdulidwe wa uzimu sufunika zambiri koma tiyenera kuuladira mu mtima mwathu mwachikhulupiliro. Sindikunena kuti okhulupilira Yesu ayenera kudulidwa mu thupi. Monga kwa ife,  mdulidwe mu thupi ulibe ntchito, koma mdulidwe wa uzimu wa chipulumutso cha myoyo yathu ndi okakamiza, poti tingakhale oyera ku machimo pokhulupilira mu ubatizo wa Yesu.

Mdulidwe wa uzimu ndi chibvomerezo choti munthu abadwe mwatsopano. Ali yense amene amakhulupilira mwa Yesu ayenera ku dulidwa mwa uzimu. Iyi ndi njira yokhayo yodula machimo mu mtima. Imatipanga ife olungama. Imatipanga ife opanda tchimo. Choncho, tiyenera kubvomera ndi chikhulupiliro ubatizo wa Yesu omwe Iye analandira kwa Yohane Mbatizi mu mtsinje wa Yordano. Mtumwi Paulo ananenanso zamdulidwe wa uzimu: “Ndipo mdulidwe uli wa mtima, mumzimu, si m’malembo ai” (Aroma 2:29). Ali yense ayenera kudulidwa mu mtima kuti alandire chikhululukiro cha machimo ake. Ichi ndi chifukwa chake mdulidwe wa uzimu uyenera kupasidwa.

Kodi machimo anu anadulidwa ndi kuikidwa pa Yesu? Ngakhale iwo amene amakhulupilira mwa Yesu mthawi ya m’Chipangano Chatsopano ayenera kudulidwa mu mtima mwa chikhulupiliro mwa Yesu. M’Chipangano Chakale khungu la nsonga linkadulidwa, koma m’Chipangano Chatsopano kukhulupilira mu mdulidwe wa uzimu mu mtima ndi chidziwitso cha unzika wa ufumu wa kumwamba. Tiyenera kudulidwa mwa uzimu pokhulupilira mu ubatizo wa Yesu.

Mtumwi Paulo ananena momveka bwino zimenezi m’Baibulo. Mulungu anapulumutsa anthu ku machimo a dziko ndi kuwapanga okhulupilira ngati anthu ake, koma Iye amakhululukira machimo pokha pokha ngati munthu wapereka machimo ake pa Yesu pokhulupilira mu ubatizo wa Yesu, monga kudula kwa nsonga la thupi. Mdulidwe wa uzimu ndi chipulumutso cha Mulungu: chimakwaniritsidwa pokhulupilira kuti Yesu anachotsa machimo a dziko kudzera mu ubatizo wake, kusenza chilango kuti apulumutse ife okhulupilira, kutipanga ife olungama, ndi kutitenga ife ngati ana ake. Mulungu amaona chikhulupiliro chathu mu ubatizo ndi mwazi wa mwana wake, ndipo amatizindikira ife ngati anthu ake. Kukhulupilira mu izi ndi mdulidwe wa uzimu komanso chikhululukiro cha machimo.Kodi Chipulumutso Chimene Yesu Anakwaniritsa Kudzera mu Ubatizo ndi Mwazi Wake ndi Chiani?


Chipulumutso Chimene Yesu Anakwaniritsa Kudzera mu Ubatizo ndi Mwazi ndi chipulumutso cha ochimwa. Mwazi wa Mwanawankhosa unali chiweruzo cha machimo ndipo ubatizo wa Yesu unali mdulidwe omwe unachotsa machimo ndi kuika pa thupi lake. Mipingo ya aKristu a lero amanyalanyaza mdulidwe wa uzimuwu. Koma, sitiyenera kunyalanyaza ubatizo wa Yesu m’Chipangano Chatsopano pamene mduliawe wa thupi m’Chipangano Chakale ndi opanda ntchito m’masiku a m’chipangano Chatsopano. Kodi mungakhulupilire mu ubatizo wa Yesu ngati ubatizowo unachotsa machimo anu onse? Ngati munyalanyaza ubatizo wa Yesu, simudzakumana ndi Uthenga Wabwino omwe Yesu anachotsera machimo anu kudzera mu ubatizo omwe analandira kwa Yohane Mbatizi kuti mubadwenso mwatsopano. 

Ndindani amene akana mdulidwe wa uzimu kudzera mu ubatizo wa Yesu omwe Mulungu akunena? Baubulo likutithandiza ife kuti tione kulumikizana pakati pa mdulidwe ndi mwazi wa Mwanawankhosa wa Paskha. Ichi ndi chinsinsi cha ubatizo wa Yesu. Mdulidwe wa uzimu ndi Uthenga Wabwino wakale wozikidwa mu ubatizo wa Yesu. Uthenga Wabwino omwe mtumwi Yohane analalikira unali Uthenga Wabwino wa madzi a ubatizo ndi mwazi wa Yesu Kristu. 1 Yohane 5:6 akuti, “Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, ndiye Yesu Kristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi. Ndipo Mzimu ndiye wakucita umboni, cifukwa Mzimu ndiye coonadi.” Baibulo likutiuza kuti Yesu sanadze ndi madzi okha kapena mwazi koma mwa madzi ndi mwazi. Nzere otsatirawu ukuchitira umboni pa chipulumutso chathu: ubatizo wa Yesu, mwazi wa Yesu pamtanda ndi kuuka kwa Yesu. Madzi a ubatizo, mwazi, ndi Mzimu Woyera ndi umboni ku Mau omwe Yesu anapulumutsira okhulupilira ku machimo ao onse. Mobwereza, chidziwitso choti tinapulumutsidwa ku machimo athu onse ndi kubadwa mwatsopano ndi ubatizo wa Yesu, mwazi wake pamtanda, komanso Mzimu Woyera.Kodi N’chifukwa Chiani Baibulo Limalankhula Zonse Ubatizo ndi Mwazi wa Yesu?


Ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake ndi Mau amene amatipanga ife kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Eksodo 12:23 akuti, “Pakuti Yehova adzapita pakatipo kukantha Aaigupto: koma pamene adzaona mwaziwo pa mphuthu pa mwamba ndi za pambali, Yehova adzapitirira pakhomopo, osalola woononga alowe m’nyumba zanu kukukanthani.” Akunena kuti Ambuye adzadutsa, zomwe zikutanthauza kuti iye adzadumpitsa chiweruzo. Ndiyeno kodi izi zikutanthauza kuti kukhulupilira mu mwazi wa Mwanawankhosa wa Paskha kungatipatse ife chikhululukiro cha machimo? Koma, Chipangano Chatsopano chinanena kuti, “kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwa Kristu Yesu; tinabatizidwa mu imfa yace?” (Aroma 6:3), “Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Kristu mudabvala Kristu.”(Agalatiya 3:27), komanso “Cimenenso cifaniziro cace cikupulumutsani tsopano, ndico ubatizo”(1 Petro 3:21). Ophunzira anapitiriza kukamba za ubatizo wa Yesu omwe Iye analandira kwa Yohane Mbatizi mu mtsinje wa Yordano m’Chipangano Chatsopano. Kukhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu ndi chikhulupiliro cholondora chomwe chimatipanga ife kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.

Kunena zoona kwa inu, kwa zaka khumi ndakhala ndi kukhulupilira mwazi wa Yesu okha. Ndinali osangalala nthawi imeneyo. Koma, popita pa nthawi, mtima wanga unali odzala ndi uchimo nthawi zonse. Ngakhale kuti ndinkakhulupilira mwa Yesu mosangalala, ndinali ndi bvutobe la uchimo. Koma pamene ndinapeza za mdulidwe wa uzimu kudzera mu ubatizo wa Yesu, ndinabadwa mwatsopano. pamene ndinabadwa mwatsopano, ndinazindikira kuti mdulidwe m’Chipangano Chakale ndi ubatizo wa Yesu m’Chipangano Chatsopano. Umu ndi m’mene ndinaika chikhulupiliro mu zimenezi. 

“Kodi ndi zolondola kukhulupilira mwazi wa Yesu pamodzi ndi ubatizo wake wa Yesu? Kodi chikhulupiliro change ndi chogona pa Baibulo?” pamene ndi nabadwa mwatsopano pokhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu, ndinayamba kudabwa chikhulupiliro change monga chonchi. “Kodi zikupanga chikhulupiliro cholondola kungokhulupilira kuti Yesu anandifera popanda ubatizo? Kodi Iye adakali Mulungu wanga ndi mpulutsi wanga kupatula kuti sindimakhulupilira kuti Yesu anachotsa machimo anga kudzera mu ubatizo?” ndinali ndi mafunso amenewa pamene ndinkawerenga Eksodo 12.

Lero, Akristu aika chikhulupiliro chao mu mwazi okha pamtanda ndi kubvomera kuti Yesu ndi mpulumutsi wao pamene akuwerenga Eksodo 12. Koma ndikuganizabe kuti ayenera kuonanso chokhulupiliro chao. Ngakhale iwo akubvomereza kuti Ambuye ndi Kristu komanso Mwana wa Mulungu wa moyo, iwo akukhalabe mu uchimo. Iwo akunena kuti anapulumutsidwa kupatula kukhala kwaobe mu uchimo, poti amakhulupilira mwa Yesu ngati mpulumutsi wao. Koma zoona ndi zakuti chikhulupiliro chotere sichogona pa choonadi. Chikhulupiliro cha olungama obadwa mwatsopano chinagona pa ubatizo ndi mwazi wa Yesu.

Ndiyeno kodi Mau a Mulungu mu Eksodo 12 akutiuza chiani ife? Pamene ndinawerenga ndimeyi mosamara. Ndinadzifunsa ndekha, “kodi sibvuto kuti Akristu akane ubatizo wa Yesu koma kungokhulupilira mu mwazi okha?” ngakhale ndisanamalize kuwerenga ndimeyi, ndinapeza choona kuti simwazi okha. Ndinatsimikiza choonadi kuti mdulidwe wa uzimu weni weni ndi otheka pamene ife takhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi pamtanda. 

Kuchoka mu Eksodo 12:47-49, ndikutha kuona Mulungu kuti anafuna iwo adulidwe asanadye Mwanawankhosa amene anaperekedwa pa phwando la Paskha. Ichi ndi chifukwa chake mu Eksodo 12:49 Mulungu akuti, “Pakhale lamulo lomweli pa wobadwa m’dziko, ndi pa mlendo wakukhala pakati pa inu.”  Mu ndime imeneyi, ndinapeza choonadi kuti iwo amene sanadulidwe sangadye Mwanawankhosa wa Paskha, amene ndi chithunzi thunzi cha Yesu Kristu. Choncho, ndinalandira Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu mu mtima mwanga pamene ndinazindikira mdulidwe wa uzimu. Ndinaima molimba pa choonadi chomwe chinapanga mtima wanga kuyera mbuu ngati matalala pobvomereza kuti machimo athu onse anaperekedwa pa Yesu kudzera mu ubatizo wake ndipo kuti Iye anasenza chilango chathu m’malo mwathu pokhetsa mwazi wake pamtanda.

Ndinazindikira choona kuti mdulidwe ndi mwazi wa Mwanawankhosa zikupezeka mu zipangano zonse kuti zibweretse Israyeli chipulumutso ku machimo a dziko lapansi: mdulidwe m’Chipangano Chakale unali ubatizo wa Yesu m’Chipangano Chatsopano: Iwo wonse ndi mdulidwe; wina wa kuthupi ndipo wina wa mu mtima. Ndipo mwazi wa Mwanwankhosa m’Chipangano Chakale unali mwazi wa Yesu pamtanda. Ndinakhulupilira kuti Yesu sanatenge chilango cha machimo ake koma potenga machimo a dziko lapansi kuzdera mu ubatizo omwe analandira kwa Yohane Mbatizi, Iye anakhala mpulumutsi wa dziko. Iwo amene akhulupilira kuti Yohane Mbatizi anapereka machimo a dziko m’malo mwa anthu onse mudziko lapansi amabvomereza zinthu ziwiri izi: ubatizo ndi mwazi wa Yesu.

Koma, iwo amene amakhulupilira mwa Yesu koma kunyalanyaza kukhulupilira mu ubatizo wake sakhulupilira mu mdulidwe wa uzimu. Pachifukwa ichi adakali mu uchimo wao ndipo amakhala kutali ndi Mulungu ngakhale iwo amakhulupilira mwa Yesu. Kodi angakhale bwanji ochimwabe pamene akhulupilira mwaYesu kwa nthawi ya itali? Kodi angakhale bwanji ndi mlandu mu dziko lino ndi kulunjika kuchionongeko? Iwo ndi omvetsa chisoni. Chifukwa sanabvomereze chilungamo choti machimo ao anachotsedwa ndi kuikidwa pa Yesu kudzera mu ubatizo wa uzimu omwe unabweretsa chipulumutso chosatha, alibe njira zina koma kukhala mu uchimo. Iwo amanena kuti analandira chikhululukiro cha machimo pokhulupilira mu mtanda okha, koma chikhulupiliro chotere sichipanga okhulupilira kukwanira. Iwo amene amakhulupilira mu mwazi okha wa Yesu sangachotseredwe machimo ao mwa chikhulupiliro. N’chifukwa chiani ziri chonchi? Chifukwa choti iwo alibe chikhulupiliro mu ubatizo wa Yesu omwe unachotsa machimo ao onse kamodzi kokha.

Pokhapo pamene takhulupilira mu zonse madzi (ubatizo wa Yesu) ndi mwazi wa Yesu molingana ndi lamulo la uzimu la chipulumutso lomwe mulungu anaika tingapulumutsidwe ku machimo. Ndipo tingakhale anthu a Mulungu. Kunalembedwa mu Baibulo, “Dziyeseni nokha, ngati muli m’cikhulupiliro, dzitsimikizeni nokha. Kapena simuzindikira kodi za inu nokha kuti Yesu Kristu ali mwa inu? Mukapanda kukhala osatsimikizidwa” (2 Akorinto 13:5). Ngati mukulimbikira pa mwazi okha wa Yesu ngati mdulidwe wa uzimu, muyenera kudziyesa nokha ngati mungapulumutsidwe kotheratu ku dziko, ndi kukonza chikhulupiliro chanu. Israyeli anapulumutsidwa ku machimo onse a dziko pamene anakhulupilira mu zonse ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake pamtanda olembedwa m’Chipangano Chatsopano. Okhulupilira mu choonadi chimenechi akhala anthu a Mulungu ndipo Mulungu akhala Mulungu wao. Mwazinthu ziwirizi, mdulidwe ndi mwazi wa Mwanawankhosa (ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake), tinakhala anthu a Mulungu. Choonadi chimenechi ndi cha Mau a kubadwa mwatsopano kudzera mwa madzi, mwazi ndi Mzimu chimene Yesu anakamba.Kodi Chikhululukiro cha Machimo Chomwe Baibulo Likunena ndi Chiani?


Yesu anasiya mpando Wake wa kumwamba, kudza pa dziko lino kulandira ubatizo kwa Yohane Mbatizi pa zaka makumi atatu, ndi kunyamula machimo a dziko lonse. Uwu ndi Uthenga Wabwino wakale. Mwazi wa Yesu ukuimilira chilango cha machimo omwe Iye anatenga kudzera mu ubatizo. Iye anadza ngati mpulumutsi wa mtundu onse ndi kupulumutsa ochimwa onse ku machimo ao onse a dziko popereka madzi ndi mwazi odzadza ndi Uthenga Wabwino wakale.

Kodi kubadwa kwathu kwatsopano kunakwaniritsidwa mwa mwazi okha? Ai tinapulumutsidwa ku uchimo mwa ubatizo wa Yesu ndi mwa wake. Ndikufuna ndifunse funso kwa iwo amene amakhulupilira mu mwazi okha wa Yesu. Kodi ochimwa amakahala olungama pokhulupilira mu mwazi okha wa Yesu? Kapena pokhulupilira mu zonse ubatizo wa Yesu analandira kwa Yohane Mbatizi mu mtsinje wa Yordano ndi mwazi pamtanda? Ndi kufuna ndi kufunse kuti cheni cheni ndi chipulumutso choona pakati pa ziwirizi.  Kodi chikhulupiliro cholondola  ndi chiti chomwe Baibulo likunena pakati pa chikhulupiliro mu mwazi okha wa Yesu ndi chikhulupiliro mu zonse ubatizo wa Yesu ndi mwazi? Kusinthika kweni kweni mwa madzi ndi Mzimu kumachokera ku chikhulupiliro choti Yesu anadza mu thupi la munthu, kuchotsa machimo athu onse kudzera mu ubatizo wake mu mtsinje wa Yordano, kunyamula machimo a dzikowo kupita nawo pamtanda, kutenga chilango cha machimo m’malo mwathu, ndu kutipulumutsa ife ku machimo onse ndi kuchiweruzo. Chikhulupiliro mu mwazi chimangokamba kuti yesu anapereka mphotho ya machimo athu; Iye anatembereredwa, kukwapulidwa, ndi kuweruzidwa kuti Iye atipulumutse ife ku chilango cha machimo athu. Koma, chikhulupiliro chotere si changwiro. Tiri ndi chinthu chimodzi chofunika kukamba bwino apa. Nanga kodi n’chifukwa chiani Yesu anapachikidwa?

Baibulo limanena kuti mphotho yache ya uchimo ndi imfa, koma Yesu sanachimweko moyo wake onse pa dziko lapansi. Chifukwa Iye ndi Mulungu Iye mwini, wa Uzimu, Iye anabwereka thupi la Maria kuti abadwe ngati munthu. Koma Iye ndi mwana wa Mulungu, amene analibe tchimo mwachibadwidwe. Choncho, monga mpulumutsi, anayenera kubatizidwa ndi Yohane Mbatizi Iye asanapachikidwe. Potenga machimo kudzera mu ubatizo, ananyamula machimo kupita nao pamtanda, kukhetsa mwazi wake ndi kukwaniritsa chipulumutso kwa ochimwa. 

Tsopano tiyeni tipeze zambiri kuchokera ku chihema pa choonadi ichi. Molingana ndi ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe m’Chipangano Chakale, Aroni kapena ochimwa ankayenera kuika manja ao pamutu pa nyama za nsembe (Mwanawankhosa kapena mbuzi) kuti apatsire machimo ao ndi kupha nyamazo ndi kuzitentha pa guwa la nsembe. Pozindikira kuti Chipangano Chakale ndi chithunzi thunzi cha Chipangano Chatsopano, kodi Yesu anatenga liti machimo a dziko asanapereke mphotho ya machimowo? Ndikufuna ndikufunseni, “kodi munapatsila machimo anu pa Yesu mwa chikhulupiliro monga m’mene munapatsila chinthu china chake kwa munthu wina?” m’Chipangano Chakale, Israyeli sankapha nyama asanaike manja ao pamutu pake. “Kuika manja” kukutanthauza “kupatsila china chake.” Mwa njira ina, pokha pokha ochimwa kapena Aroni aike manja ao pa nsembe za nyama ndi kupatsila machimo pa izo, sakanapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu.

Levitiko 1 akukamba za ‘kuika dzanja pamutu pa nyama’ ndime yonse. Iwo akanapulumutsidwa ku machimo ao popereka machimo ao mwa kuika manja pa nsembe ya mwanawankhosa kapena mbuzi ndi kupha izo ndiponso popereka mwazi wake ndi nyama kwa Mulungu. M’Chipanagano Chakale, Israyeli anapulumutsidwanso mwa chikhulupiliro. 

Mu Eksodo 12, mdulidwe ndi mwazi wa mwanawankhosa zatchulidwa. Ndipo mu Eksodo 20, muli malamulo khumi. Ndipo ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe ku chihema limatsata malamulowo. Nthawi zonse Israyeli akanapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu, a nsembe ankayenera kupatsila machimo a chaka chonse a Israyeli pa nyama ya nsembe, ndipo ankadula khosi lake, kuwaza pa guwa la nsembe lopsereza ndi kuthila mwazi otsala pansi pa guwa.

Momwemonso, ochimwa ife tingapumutsidwe pokhulupilira mu madzi ndi mwazi wa Yesu. 1 Yohane 5:1-10 akunena kuti ubatizo ndi mwazi(mtanda) wa Yesu umapulumutsa ochimwa. Mwanjira ina, ochimwa angalandire chikhululukiro cha machimo pokhulupilira ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Ubatizo wa Yesu, mwazi wake ndi Mzimu muli chilungamo cha choonadi cha kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.

Kodi timalandira chikhululukiro cha machimo pongokhulupilira mu mwazi wa Kristu okha? Iwo amene amayesa kubadwa mwatsopano pokhulupilira mu mwazi okha wa Yesu pamtanda ali ndi uchimobe mu mtima mwao. Koma, tingapulumutsidwe ku machimo onse pokhulupilira mu ubatizo wa Yesu omwe uli mdulidwe wa uzimu, omwe ukufanana ndi mdulidwe wa thupi m’Chipangano Chakale. Mpingo uli onse uli ndi  chikhulupiliro chosiyana mwa Yesu. Ndikuziwa kuti chikhulupiliro chao ndi chosiyana. Ndikuziwa kuti chikhulupiliro chao sicholondola. Mpingo wa Presbyterian ndi nkhala pakati wa chiphunzitso cha kukonzedweratu; mpingo wa Methodist ndi nkhala pakati wa Arminianism omwe ndi ofanana ndi umunthu; mpingo wa Baptist umalimbikira ubatizo wakumizidwa; komanso mpingo wa Holiness umaona pa za moyo opembedza. Koma kodi Baibulo likutiuza chiani pa za kubadwa mwatsopano? Baibulo likutchula ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Iwo amene amafuna choonadi mogwirizana ndi Baibulo amapeza unzake wa ndime iliyonse kuchokera mu Chipangano Chakale komanso Chatsopano ndi kukhulupilira  bwino bwino.    

  


Kodi Chinsinsi Cha Ubatizo wa Yesu ndi Chiani?


Ubatizo omwe Yesu analandira unali mdulidwe wa uzimu kwa okhulupilira  mu ubatizo Wake. Mulungu ananena mu Chipangano Chakale kuti adzachotsa onse osadulidwa pamaso pake. Tiyenera kukhulupilira kuti mdulidwe wa uzimu pa chipulumutso m’Chipangano Chatsopan ndi ubatizo wa Yesu. Yesu analandira ubatizo kwa Yohane Mbatizi kuti apulumutse mtundu onse ku uchimo, mwa iwo tinatha kudulidwa mu uzimu mu mitima yathu pokhulupilira mu ubatizo wake. Tiyenera kuganiza mwakuya chifukwa chimene Yesu ankayenera kulandira ubatizo kwa Yohane Mbatizi.

 Zochikitika pa ubatizo wa Yesu zinalembedwa mu ndime kuchokera Mateyu 3:13. “Pamenepo Yesu anacokera ku Galileya nadza ku Yordano kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye. Koma Yohane anati amkanize, nanena, ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi? Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti tiyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero. Pamenepo anamlola Iye.” (Mateyu 3:13-15). Yesu anabatizidwa ndi madzi mu mtsinje wa Yordano, omwe umadziwika kuti “mtsinje wa imfa.” Yohane Mbatizi anaika manja ake pamutu pa Yesu, ndi kumulola iye kumizidwa. Uwu ndi ubatizo olondola, ndiye kunena kuti, “ubatizo mwa kumizidwa.” Kubatiza, “baptizo” mu chi Greek kutanthauza kumiza kapena kunyika pansi pa madzi. Yesu anayenera kutenga machimo adziko kudzera mu ubatizo omwe Iye analandira njira yakuika manja monga m’Chipangano Chakale. 

Popeza ubatizo omwe Yesu analandira kwa Yohane Mbatizi unali mdulidwe wa uzimu kwa anthu onse, Iye ananena asanabatizidwe, “Balola tsopano, pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero.” Kunali koyenera kuti Yesu achotse tchimo la dziko ndikukhala mpulumutsi wa ochimwa onse, Mau amene apanga kubadwa mwatsopano. chinthu choyamba chimene Yesu anachita pamene anayamba moyo wake poonekera kunali kubatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Ndanena kuti kubatiza, ‘baptizo’ mu chi Greek kukutanthauza kumiza kapena kunyika pansi pa madzi. Mau amenewa akutanthauzanso “kutsuka, kukwirira, kusamutsa, kapena kupatsira.” Mu Chipangano Chakale, Israyeli anasunga Yom Kippur (Tsiku La Chitetezero cha machimo) patsiku la khumi la mwezi wachisanu ndi chiwiri chaka chiri chonse poika machimo ao a chaka chonse pa mbuzi ziwiri. Akatha kuika machimo ao, ankampha mbuzi ndi kupereka mwazi wake ngati nsembe. Kenako ankabweretsa mbuzi ina yamoyo patsogolo pa Israyeli, kuika machimo ao pa iyo kudzera mu kuika manja a mkulu wansembe ndipo ankaisiya yokha mbuziyo mchipululu kuti ife. Ndondomeko yake yonse inalembedwa mu Levitiko 16. Patsiku limenelo mkulu wansembe ankaika manja ake pamutu pa mbuzi ndi kupatsila machimo onse a chaka chonse a Israyeli pa iyo.

Yesu anachotsanso machimo onse adziko kamodzi kokha kudzera mu ubatizo pamene Iye anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi, oimilira wa anthu onse komanso m’modzi wa mbadwo wa Aroni mkulu wansembe. Tsiku lotsatira patatha ubatizo wake, Yohane Mbatizi anachitira umboni za Yesu kunena kuti, “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi”(Yohane 1:29).  Pamene Yesu anabatizidwa, pamene machimo onse adziko anabwera pa Iye, Iye ananyamula machimo a dziko ngati Mwanawankhosa wa Mulungu, kuyenda molunjika mtanda ndi kulipira mphotho ya machimo onse kuti apulumutse mtundu onse ku machimo. Motero, mdulidwe wa uzimu kwa anthu onse unakwaniritsidwa. Iwo amene alandira ubatizo wa Yesu (mdulidwe m’Chipangano Chakale) ndi mwazi wake pamtanda (mwazi wa mwanawankhosa wa Paskha) ngati chipulumutso chao angapulumutsidwe ku machimo ao onse. Yesu anapulumutsa ochimwa onse mwa ubatizo wake ndi mwazi wake. Uwu ndi mdulidwe wa uzimu omwe umapatsa okhulupilira ali yense chikhululukiro cha machimo.Kodi Chipulumutso Chinakwaniritsidwa Mwa Mwazi Okha? Ai!


Mulungu akutiuza zimenezi momveka bwino mu 1 Yohane 5. “Pakuti ciri conse cabadwa mwa Mulungu cililaka dziko lapansi; ndipo ici ndi cilako tililaka naco dziko lapansi, ndico cikhulupiriro cathu. Koma ndani iye wolilaka dziko lapansi, koma iye amene akhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu. Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, ndiye Yesu Kristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi. Ndipo Mzimu ndiye wakucita umboni, cifukwa Mzimu ndiye coonadi. Pakuti pali atatu akucita umboni, Mzimu, madzi ndi mwazi; ndipo iwo atatu ali mmodzi” (1 Yohane 5:4-8).

Kodi mukuganiza kuti chizindikiro choti mwapulumutsidwa ku machimo a dziko ndi chiani? Ndi chikhulupiliro mu Mwana wa Mulungu, amene anadza mwa madzi ndi mwazi. Ndi chiani chimatipangitsa ife kugonjetsa dziko? Baibulo likunena momveka bwino apa, “Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, ndiye Yesu Kristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi. Ndipo Mzimu ndiye wakucita umboni, cifukwa Mzimu ndiye coonadi. Pakuti pali atatu akucita umboni, Mzimu, madzi ndi mwazi; ndipo iwo atatu ali mmodzi” (1 Yohane 5:6-8).

Yesu Kristu anadza pa dziko lino, analandira ubatizo, kukhetsa mwazi wake ndi kupulumutsa ife ku imfa. Mzimu Woyera ndi mboni kuchilungamo choti Mulungu Namalenga anakhala mpulumutsi. Uthenga Wabwino wa kale ndi umboni wa madzi ndi Mzimu omwe Yesu anachotsa machimo athu onse kudzera mu ubatizo wake mu mtsinje wa Yordano; kukhetsa mwazi wake pamtanda, kuzunzika ndi chilango kupulumutsa ife okhulupilira ku machimo athu onse.Kodi Madzi ndi Mwazi Ngati Umboni ku Chikhululukiro Cha Machimo Ndi Chiani?


Madzi mu ndime ya pamwambayi akutanthauza ubatizo wa Yesu. Ubatizo wake unali chimodzi modzi ndi mdulidwe m’Chipangano Chakale. Ubatizo wa Yesu ndi mnzake wa mdulidwe m’Chipangano Chakale. Ndi chidziwitso kuti machimo onse a ochimwa anachotsedwa ndi kuikidwa pa Yesu. Tsopano ali yense amene wakhulupilira choncho angaime pamaso pa Mulungu molimba mtima ndi kubvomereza, “Yesu ndi Mpulumutsi wanga. Iye ndi Mbuye wanga. Sindilinso mu uchimo chifukwa ndikukhulupilira mu Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu, ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Ndine mwana wa Ambuye. Mulungu ndi Mulungu wanga. Yesu ndi Ambuye wanga.” Chifukwa chokhacho chimene tinganenere zimenezi n’chakuti tiri ndi chikhulupiliro mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Chimatipangitsa ife kubadwa mwatsopano ndi chiani? Ndi umboni mu mtima mwathu, ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake pamtanda, muli Uthenga Wabwino wa choonadi umene umatipangitsa ife kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.

Okondedwa Akristu anzanga, kodi ndi mwa mwazi okha wa Yesu Kristu kuti ochimwa aike chikhulupiliro chao mwa Yesu ndi kubvomera Iye ngati Mpulumutsi wao? Si mwa mwazi okha wa Yesu. Ndi mwa madzi ndi mwazi; madzi ndi Mzimu.

Tiyeni tiyang’ane mu Baibulo za madzi, omwe ndi ubatizo wa Yesu. Kunalembedwa mu 1 Petro 3:21-22, “Cimenenso cifaniziro cace cikupumutsani tsopano, ndico ubatizo, kosati kutaya kwa litsoro lace la thupi, komatu funso lace la cikumbu mtima cokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Kristu; amene akhala pa dzanja lamanja la Mulungu, atalowa m’Mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zomgonjera.”   

Mtumwi Petro anati ubatizo wa Yesu ndi chifaniziro cha chipulumutso, komanso chitsimikizo cha chipulumutso chake chinagona mu ubatizo wa Yesu. Ubatizao wa Yesu unali mdulidwe m’Chipangano Chakale. Monga m’mene a Israyeli analemekezera Mau a Mulungu ndi kuchita mdulidwe kuti akhale ana a Mulungu, ubatizo wa Yesu unachotsa machimo onse a ochimwa; choncho, mdulidwe m’Chipangano Chakale ndi ubatizo wa Yesu ukutanthauza chinthu chimodzi. Kodi mumakhulupilira umboni oti ubatizo wa Yesu ndi mdulidwe m’Chipangano Chakale? 1 Petro 3:21 akunena kuti ubatizo wa Yesu ndi chifaniziro wa chipulumutso, kodi mudzaima molimbanabe ndi Mau a Mulungu?

Kodi ali yense mu dziko lino angakhale bwanji opanda machimo? Koma Yesu anabatizidwa chifukwa cha chipulumutso chathu ndipo anakwaniritsa chilungamo chonse. Mateyu 3:15 akuti, “Balola tsopano pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero.” Chifukwa machimo onse a mtundu onse a anthu anaikidwa pamutu pa Yesu, ali yense wakhulupilira mu ubatizo wake wakhala munthu opanda tchimo ndi olungama pobvomereza chilungamo choti Yesu anachotsa machimo ake onse kudzera mu ubatizo wake kamodzi kokha. Yesu Kristu ananyamula machimo adziko lapansi kukhetsa mwazi wake ponyamula chilango cha tchimo pamtanda.

Zinthu ziwiri zomwe zimapulumutsa ochimwa ku machimo onse ndi madzi ndi mwazi. Ndipo Yesu anakwaniritsa ziwirizi nthawi yake ya zaka makumi atatu ndi zitatu za moyo wake pa dziko lino. Kodi mumakhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu? Yohane 1:29 akunena kuti, “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa cimo lace la dziko lapansi!” Yesu analandira ubatizo, kuchotsa machimo onse a dziko ndi kunyamulira machimowo molunjika mtanda. Ambuye ndi Mwana wa Mulungu, Mlengi ndipo komabe Iye anakwaniritsa pangano la mdulidwe m’Chipangano Chakale kudzera mu ubatizo. Iwo amene alandira madzi a ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake adzabadwa mwatsopano mwa Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu. Ambuye kenako adzakhala Ambuye wao. Zikomo, Ambuye. Aleluya! Ambuye anakwaniritsa lonjezo lake: Iye anatipulumutsa ife ku machimo a dziko lapansi.

“Cimenenso cifaniziro cace cikupumutsani tsopano, ndico ubatizo, (kosati kutaya kwa litsoro lace la thupi, komatu funso lace la cikumbu mtima cokoma kwa Mulungu)” (1 Petro 3:21)

Sizikutanthauza kuti sitichita chili chonse choipa ndi thupi lathu chifukwa choti timakhulupilira mwa Yesu ngati Mpulumutsi wathu. Ngakhale timachimwabe mu thupi, talandira chikhululukiro cha machimo pokhulupilira kuti ubatizo wa Yesu unachotsa machimo athu onse, Iye anasenza chilango cha machimo athu onse, ndipo ubatizo ndi mwazi wa Yesu wabweretsa chipulumutso kwa ife okhulupilira.

Kubadwa mwatsopano polandira Ambuye ngati Mpulumutsi wathu kumatenga malo mu mtima mwathu ndi Mzimu. Chimodzi modzinso chikhululukiro cha machimo. Komabe, sitingadzithandizebe tokha koma kupezeka m’machitidwe onyansa ndi kuchimwa mu thupi ngakhale tabadwa mwatsopano mu mtima mwathu, koma ngakhale machimo ameneo anakhululukidwa kale. Ubatizo wa Yesu umachitira umboni kwa iwo amene anapulumutsidwa. Tinakhala olungama kudzera mu Uthenga Wabwino wa kale wa madzi ndi Mzimu pamene takhulupilira mu choonadi cha chipulumutso chomwe chimachitira umboni kumachimo onse kuti anaperekedwa pa Yesu pa nthawi ya ubatizo wake. Ichi ndi chikhulupiliro cha Abrahamu m’Chipangano Chakale ndi chilungamo mwa chikhulupiliro chomwe Paulo ananena, komanso chifaniziro cha chipulumutso chomwe Petro anakamba.

Kodi chipulumutso chanu chinakwaniritsidwa mwa mwazi okha wa Yesu? Ai. Kodi ndi mwa madzi okha? Ai. Chipulumutso ku machimo chakwaniritsidwa mwa madzi ndi mwazi. Yesu Mwana wa Mulungu anadza pa dziko lino lapansi, kuchotsa machimo athu onse, kunyamula machimo kupita nao pamtanda ndi kusenza chilango cha machimo kuti Iye apulumutse ochimwa onse. Timalandira chipulumutso pokhulupilira kuti Yesu Kristu anachotsa machimo athu onse kudzera mu ubatizo wake ndi mwazi; kubvutika ndi chilango chathu kuti ochimwa onse apulumutsidwe.

Monga kunalembedwera, “Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo cinawerengedwa kwa iye cilungamo” (Aroma 4:3), timalandira chipulumutso pamene takhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Ambuye anadza pa dziko lino, kuchotsa machimo onse a dziko kudzera mu ubatizo wake, ndi kupereka mphotho ya machimowo pokhetsa mwazi wake pamtanda. Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu unapulumutsa ife ku machimo a dziko. Iwo a ife amene takhulupilira mu choonadi ichi talandira chikhululukiro cha machimo chomwe chatipanga ife kubadwa mwatsopano. Tingapulumutsidwe ku machimo ndi kubadwa mwatsopano polandira Uthenga Wabwino wa chikhululukiro cha machimo.

Yohane 1:12 akuti, “koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lace.” Kodi mumakhulupilira Yesu ngati Mpulumutsi wanu, amene anakupulumutsani ku machimo kudzera mu ubatizo wake ndi mwazi? Muyenera kulandira chipulumutso chimene Mwana wa Mulungu anakwaniritsa kudzera mu madzi ndi mwazi. Kodi Mulungu akufuna kuti ife tichite chiani? Iye akufuna ife tikhulupilire mwa Mwana wake. Ndipo Iye akufuna ife kuti tilandire chikhululukiro cha machimo mwa chikhulupiliro. Yesu anadza pa dziko lino mu thupi kuti apulumutse ochimwa onse; pa zaka makumi atatu iye analandira ubatizo kuchotsa machimo a dziko kuti apatse mdulidwe wa uzimu; ndipo Iye anafa pamtanda ngati Mwanawankhosa wa Mulungu pokhetsa mwazi wake. Kukhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu ndi chikhulupiliro chomwe chimakupangani kubadwa mwatsopano. Ambuye anakhala mtetezi wa ochimwa onse kudzera mu ubatizo wake ndi mwazi. Umu ndi m’mene Iye anatipulumutsila ife okhulupilira ku machimo athu onse. Ichi ndi chikhulupiliro chomwe chimatipanga ife kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.

Chilungamo chimene chimatipanga ife kulungama mwa chikhulupiliro ndi Uthenga Wabwino wa madzi ndi mwazi. Kodi ndi mwa mwazi okha wa Kristu? Ai. Ndi mwa mwazi ndi madzi. Baibulo limatiuza ife kuti chipulumutso ku uchimo si mwa mwazi wa Yesu okha. Kunalembedwa kuti ubatizo ndi mwazi wa Yesu unabweretsa chipulumutso kwa ife. Ubatizo wa Yesu ukutanthauza mdulidwe wa uzimu. Ichi ndi choonadi cha chipulumutso chomwe chimachotsa machimo athu onse. Iye analangidwa chifukwa cha ochimwa, inu ndi ine. Iye anatipulumutsa ife kuchilango pamene ife tinakhulupilira mu Uthenga wabwino wa chipulumutso, ubatizo ndi mwazi, mu mtima mwathu. Timalandira chipulumutso ku machimo a dziko mwa chikhulupiliro. Machimo athu anakhululukidwa pamene takhulupilira ubatizo ndi mwazi wa Yesu Kristu chatipatsa ife chipulumutso cha ngwiro. Kodi mukukhulupilira mu zimenezi? Ndikuyembekeza inu kukhulupilira mu Uthenga Wabwino wa  madzi ndi Mzimu. Ndikupemphera kuti inu muike chikhulupiliro chanu mu Uthenga Wabwino ndi kulandira moyo wosatha.Ngakhale Mtumwi Paulo Anakhulupilira Zimenezi


Mtumwi Paulo anati, “Mdulidwe uli wa mtima, mumzimu, si m’malembo ai” (Aroma 2:29). Timalandira mdulidwe wa uzimu pokhulupilira kuti Yesu anadza padziko lino mu thupi la munthu, kuchotsa machimo onse adziko lapansi polandira ubatizo, ndi kukhetsa mwazi wake pamtanda, ndi kuukanso kwa akufa. Paulo anati mdulidwe wa uzimu uyenera kuchitika mu mtima. Mdulidwe wa mitima yathu umachitika pamene takhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Ngati mukufuna kudulidwa mu uzimu mu mtima mwanu, muyenera kulandira Uthenga Wabwino wa ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Mwanjira yokhayi, mungakhale nzika yeni yeni ya Mulungu. Mdulidwe wa mtima ndi kukhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Olungama ndi anthu amene akhulupilira mu ubatizo wa Yesu pamodzi ndi mwazi Wake. Kodi Yohane Mbatizi Anatumidwa ndi Mulungu?


Timadabwa, “kodi Yohane Mbatizi, amene anabatiza Yesu ndindani?”  Yohane Mbatizi yemwe anali oimilira mtundu onse wa anthu. Mateyu 11:11 akukamba zimenezi. Yesu anati, “Indetu ndinena kwa inu, sanauke wakubadwa mwa akazi munthu wamkuru woposa Yohane Mbatizi; koma iye amene ali wocepa mu Ufumu wa kumwamba amkulira iye. Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa kumwamba uli wokangamizidwa, ndipo okangamirawo aukwatula ndi mphamvu. Pakuti aneneri onse ndi cilamulo cinanenera kufikira pa Yohane. Ndipo ngati mufuna kulandira, uyu ndiye Eliya amene amati akudza” (Mateyu 11:11-14).

Yesu anati sanauke munthu wamkulu oposa Yohane Mbatizi mwa iwo obadwa mwa akazi. Ndipo Iye anapitiriza, “Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa kumwamba uli wokangamizidwa, ndipo okangamirawo aukwatula ndi mphamvu. Pakuti aneneri onse ndi cilamulo cinanenera kufikira pa Yohane.” Masiku a Yohane Mbatizi anali mbadwo omaliza wa Chipangano Chakale, nthawi ya pangano la Mulungu. Ndi chifukwa Yesu Kristu (wamkulu amene anakwaniritsa pangano) anaonekera mu mbiri ya umunthu.

Nanga ndani amene adzakwaniritsa pangano la Chipangano Chakale? Iwo ndi Yohane Mbatizi ndi Yesu. Yohane Mbatizi anapatsira machimo onse adziko pa Yesu. Kodi mneneri omaliza ndani m’Chipangano Chakale? Kodi mkulu wansembe otsiliza ndindani? Kodi mbeu ya Aroni ndindani? Yesu mwini anachitira umboni kuti ndi Yohane Mbatizi. Iye ndi oimilira anthu onse komanso munthu wamkulu obadwa pakati pa akazi. Mose, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo-iwo onse anabadwa mwa akazi. Koma kodi mwa amuna onse m’Chipangano Chakale ndi chatsopano, ndindani wamkulu wobadwa mwa anthu onse? Palibe oposa Yohane Mbatizi. Iye ndi m’neneri omariza m’Chipangano Chakale, komanso mtumiki wa Mulungu otumizidwa ndi Iye. Choncho, iye amaenera kupatsira machimo onse pa Yesu monga m’mene mkulu wansembe m’Chipangano Chakale ankaikira manja ake pa mwanawankhosa kuti apatsire machimo a Israyeli. Iye anali mtumiki wa Mulungu amene anakwaniritsa mdulidwe wa mtima pobatiza Yesu.

Ndi kufuna inu mutenga mwazi wa Yesu pamodzi ndi ubatizo wake ngati umboni wa chikhululukiro cha machimo. Yesu anachotsa kale machimo onse a adziko kudzera mu ubatizo ndi kulipira chilango cha machimo onsewo. Uthenga Wabwinowo ukutanthauza kwa ife kuti tikhulupilire zomwe Yesu anachita kale. Ngati tikhulupilira mu Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu, omwe unatipanganso ife, takhala mbeu ya uzimu ya Abrahamu ndipo tingalowe mbadwo wa Yesu Kristu. Ndikukhulupilira kuti ena a inu mwalowa mu mbadwo wa Yesu Kristu mwa chikhulupiliro, koma ena adakali kunja. Ndipo dzuwa likufuna kulowa. Muyenera kuika chikhulupiliro chanu mu ubatizo wa Yesu ndi kubwera mu mbadwo wa Yesu mwa change. Chikhulupiliro chanu mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu chidzakhala kudzodzedwa kwa uzimu ku chipulumutso chanu. Ndikukhulupilira kuti mukumvetsetsa chinsinsi cha chipulumutso kuti kudzodzedwa kwa uzimu kwakonzedwa mwa chikhulupiliro chokha mu Uthenga Wabwino wa ubatizo ndi mwazi wa Yesu.Kodi Yesu Anabatizidwira Ndani?


Kunalembedwa, “Koma Yohane anati amkanize, nanena, ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi? Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti tiyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero. Pamenepo anamlola Iye.” (Mateyu 3:14-15). Yesu analandira ubatizo kuchotsa machimo onse adziko lapansi kwa anthu onse. Yesu ndi Mwana wa Mulungu komanso Iye ndi Mulungu wathu. Iye ndi Mlengi wathu. Iye anadza pa dziko lino ndi chifuniro cha Mulungu kutipanga ife anthu ake. Kodi uneneri onenedwa m’Chipangano Chakale unkalosera ndani? Onse unali wa za Yesu Kristu. Uneneri onse ukukamba za m’mene Yesu adzabwerere pa dziko lino komanso m’mene adzachotsere machimo.

Monga mwa uneneri, Yesu anadza pa dziko lino, ndi kuchotsa machimo onse amene anachitidwa komanso amene adzachitidwe ndi anthu onse, kuchokera kwa Adamu ndi Hava kufikira kwa munthu omaliza pa dziko lapansi. Tsopano, landirani chipulumutso chimene Yesu anakwaniritsa kudzera mu ubatizo wake ndi mwazi. Kodi simukumvetsetsa kuti ichi ndiye choonadi? Kodi mudakali mu machimowabe? “Balola tsopano: pakuti tiyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero.” Anatero Yesu asanabatizidwe ndi Yohane Mbatizi. Mau onena kuti ‘kubatiza’ akutanthauza ‘kutsuka.’ Kodi machimo athu angatsukidwe bwanji kudzera mu ubatizo wa Yesu? Chifukwa machimo athu onse anaikidwa pamutu pa Yesu. Ndipo machimo a mitima yathu anatsukidwa.

Chifukwa machimo athu onse anaikidwa pa Yesu kudzera mu ubatizo, iwo amene alandira zimenezi mu mtima mwao alandira chipulumutso ku uchimo. Chifukwa ‘ubatizo’ ukutanthauza ‘kutsuka kwa machimo,’ kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi kulandira mdulidwe wa uzimu mu nthawi Iyi ya Chipangano Chatsopano. “Ndipo mdulidwe uli wa mtima.” Pamene takhulupilira mu mtima mwathu kuti machimo athu onse anaperekedwa pa Yesu mwa ubatizo wake, mdulidwe wa uzimu wachitika. Mdulidwe wa mtima ndi kubvomereza ubatizo wa Yesu kuti anachotsa machimo athu onse. Kodi munadulidwadi mu mtima mwanu? Pamene mtima wanu wadulidwa, machimo anu onse adzatsukidwa. Umu ndi mumene chilungamo chonse cha Mulungu, kapena kuti, chipulumutso cha ochimwa onse, chinakwaniritsidwa.

Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Yohane Mbatizi anaika manja ake pamutu pa Yesu kuti apatsire machimo a dziko pa Yesu monga akulu akulu a nsembe m’Chipangano Chakale ankaika manja ao pamitu ya nyama za nsembe kuti apatsire machimo onse a Israyeli. Masiku a m’Chipangano Chakale, a Israyeli ankabweretsa nyama zopanda chirema, kuika manja ao pamitu pa nyamazo, kupereka machimo ao pa izo, kupha ndi kupereka mwazi wa nyamazo ku a nsembe kuti alandire chikhululukiro cha machimo ao. Yesu anabatizidwa kutenga machimo pa thupi lake.

Pamene Ambuye anatenga machimo onse a dziko, Iye anaturuka m’madzi. Iye anamira m’madzi. Izi zikutanthauza Imfa ndi chiweruzo cha ochimwa. Kumizidwa kwake kukutanthauza mwazi wake pamtanda ku chilango cha machimo athu. Kenako Iye anaturuka m’madzi. Izi zikutanthauza kuuka kwake. Yesu anauka kwa akufa patsiku lachitatu. Ichi ndi chidziwitso kuti Yesu ndi Mulungu wathu ndipo Iye anatipulumutsa ife mwa ngwiro ku uchimo. Ubatizo wa Yesu, mwazi wake pamtanda, komanso kuuka kwake m’masiku atatu ndi kukhala kwake kudzanja la manja la mpando wa Mulungu-zonse Izi zikutsimikiza kuti Iye anapulumutsa anthu onse ku uchimo. Kodi mukukhulupilira zimenezi? Ndikufuna Inu mutenge Mau achitsimikizowa mu mtima mwanu. Ichi ndi choonadi. Ngati mwalandira Ambuye mu mtima mwanu, mudzalandira chipulumutso ku machimo anu onse monga kunalembedwa, “Koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulipirira dzina lace” (Yohane 1:12).

Okondedwa Akristu anzanga, kodi mukudziwa tsopano chifukwa chimene Yesu anayenera kubatizidwira? Kodi mukukhulupilira mu zimenezi tsopano? Ubatizo wa Yesu unalu otenga machimo onse a anthu. Ndiye mdulidwe m’Chipangano Chatsopano. Ubatizo wa Yesu! Ndiye mdulidwe wa uzimu. Pachifukwa Icho, mtumwi Paulo anati mdulidwe uyenera kukhala wa mtima. Yesu anapulumutsa Ife tonse ndi ubatizo wake komanso mwazi wake kuti tisakaike chidziwitso choti machimo athu anachotsedwa. Tsopano tiri ndi chikhulupiliro chokha chonena ‘Inde’ m’maganizo ndi mtima mwathu. Kodi izi ndi zoona? Kodi mukubvomereza?Kodi Mukukhulupilira Choncho?


Ife panalibe koma papita zaka pafupi fupi 2000 pamene Yesu anabatizidwa ndi kupachikidwa. Chinthu chomwe tiyenera kuchita ndi kungobvomera choonadi cha madzi ndi mwazi wa Yesu. “Ndipo mdulidwe uli wa mtima.” Tinadulidwa m’maganizo athu ndi mtima mwa chikhulupiliro. Tinalandira chipulumutso mwa chikhulupiliro m’Chipangano Chakale, mbeu ya Abrahamu, yodulidwa, inapulumutsidwa mwa mwazi wa mwanawankhosa wa Paskha omwe anapaka pa mphutu ya pamwamba ndi ya zambali m’nyumba zao.

Iwo amene akhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu ngati chipulumutso alibe nkhawa zodandaula padziko lino, ngakahale mu nthawi ya chiweruzo cha Mulungu. Koma, kwa iwo amene sanalandire ubatizo ndi mwazi wa Yesu mu mtima, chiweruzo chopanda chifundo cha Mulungu chidzagwera pa iwo. Kodi n’chifukwa chiani Akristu ambiri akusochera? Ndi chifukwa chiani akubvutika? Chifukwa iwo anakhulupilira kuti mwazi wa Yesu unawapulumutsa iwo posadziwa choonadi cha ubatizo ndi mwazi wa Yesu.

Kodi chipulumutso chimakwaniritsidwa mwa mwazi okha wa Yesu? Kodi Baibulo linanena kuti linakwaniritsidwa mwa mwazi okha? Kodi Chipangano Chakale ndi Chipanagano Chatsopano zikunena chiani? Malembo akutiuza ife kuti chipulumutso chathu si cha mwa mwazi okha wa Mwanawankhosa komanso mwa ubatizo wa Yesu (1 Yohane 5:6-8). M’Chipangano Chakale Israyeli anakhala anthu a Mulungu mwa mdulidwe wa thupi lawo ndi mwa mwazi wa mwanawankhosa wa Paskha. M’Chipangano Chatsopano, kunanenedwa kuti chipulumutso chimakwaniritsidwa ndi ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Ichi ndi choonadi cha chipulumutso chimene Ambuye anakwaniritsa. Izi ndiye zimene zinalembedwa mu Baibulo. Ndiyeno, kodi Baibulo ndi mau a munthu? Kodi Baibulo si Mau a Mulungu? 

Kodi mumakhulupilira mu mwazi okha wa Yesu? Ngati ndi choncho, ndiye kuti mudakali mu uchimo. Muyenera kutembenuka ku chikhulupiliro chanu cholakwika. Bvomerezani kuti munanyalanyaza ubatizo wa Yesu mu mtsinje wa Yordano, ndi kulapa. Muyenera tsopano kubvomera chilungamo kuti Ambuye anachotsa machimo adziko kuphatikiza anu kudzera mu ubatizo wake. Mungapulumutsidwe pokhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu, Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu. 

Kodi mumadalira mwa mwazi okha wa Yesu? Ndiye kuti mudakali mu uchimo. Mungadzimve kuyeretsedwa pamene simunachimwe, koma mungadzimve ochimwa pamene mwachita tchimo. Kudzimva kwanu sikuli pa Mau a Mulungu, koma kuli pa thupi lanu. Koma, nthawi siinathe kuti muike chikhulupiliro chanu mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu pofuna kuti mudulidwe mu mtima mwanu ndi kumasulidwa ku machimo anu onse. ‘Kumasulidwa ku machimo onse’ kukutanthauza kupulumutsidwa ku machimo onse pokhulupilira mu Uthenga Wabwino wakale wa ubatizo ndi mwazi wa Yesu.

Kodi mumakhulupilira ubatizo ndi mwazi wa Yesu monga nkhwangwa za chipulumutso ku machimo anu onse? Pamene mudzakhulupilire mu izi, mudzazindikira chimene chidzachitike kwa inu pang’no ndi pang’ono. Ndipo mudzapeza mtendere mu ntima mwanu. Kenako mudzakhala olungama osati mwa ntchito zanu koma mwa Mau a Mulungu. Ngati wina wa inu amadalira mwa mwazi okha wa Yesu, ndikufuna ndikufunseni funso: “kodi chipulumutso chanu ku machimo chinapezeka  mwa mwazi okha wa Yesu?” Chipulumutso ku machimo sichimapezeka mwa mwazi okha wa Yesu. Ndi mwa ubatizo ndi mwazi wa Yesu, ndiye, mwa Uthenga Wabwino wakale.

Chipulumutso ku machimo chinakwaniritsidwa mwa Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu omwe mukupezeka ubatizo wa Yesu omwe analandira kwa Yohane Mbatizi komanso mwazi Wake. Mzimu ukutanthauza Mulungu. Mulungu anadza padziko lino mwa thupi la munthu. “Ndipo udzamucha dzina lace Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ace ku machimo ao” (Mateyu 1:21). Uwu unali uneneri. Mulungu ananena kudzera mwa mngelo Wake, “Onani namwali adzaima, nadzabala Mwana wamwamuna, ndipo adzamucha dzina lace, Emanueli; ndilo losandulika, Mulungu nafe.”

Mulungu anadza pa dziko lino mu thupi la munthu ndi kulandira ubatizo omwe unachotsa machimo a ochimwa onse. Ndipo Iye anasenza mphotho ya machimowo pamtanda. Motero, Iye  anapulumutsa ochimwa. Ichi ndi choonadi chachipulumutso chomwe chinakwaniritsidwa mwa madzi ndi mwazi. “Kodi mumalandira chipulumutso mwa mwazi okha wa Yesu?” Ai. Talandira chipulumutso mwa zonse ubatizo ndi mwazi wa Yesu Kristu.

Chifukwa chimene kuli aneneri onyenga ambiri ndi ampatuko mu chi Kristu ndi chakuti aKristu ambiri sadziwa za madzi a ubatizo wa Yesu. Mu Yohane 8 Yesu akuti, “ndipo mudzazindikira coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulan” (Yohane 8:32). Tiyenera kumvetsetsa choonadi. Tiyenera kufufuza chifukwa chimene Yesu anakambira za ubatizo Wake mu Baibulo ndipo tiyenera kuika chikhulupiliro chathu mu ubatizowo. Tiyeneranso kumvetsetsa chifukwa chimene Mulungu analamulira a Israyeli kuti adzidulidwa komanso chifukwa chimene Mulungu anatchulira mwazi wa mwanawankhosa wa Paskha. Ngati simukhulupilira mwa chimodzi cha zimenezi, simuzadziwa choonadi chimene chingakupangitseni kubadwa mwatsopano. Yesu anati, “Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu” (Yohane 3:5).  Baibulo ndi buku la chinsinsi pa chipulumutso. Kodi ndi mwa mwazi wa Yesu okha? Mtumwi Paulo anakamba za ubatizo wa Yesu mobwereza bwereza m’makalata ake, mwachitsanzo, mu Aroma 6 ndi mu Agalatiya 3.

Tiyeni tione mu Aroma 6 poyamba. “Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwa Kristu Yesu; tinabatizidwa mu imfa yace? Cifukwa cace tinaikidwa m’manda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo kulowa muimfa; kuti monga Kristu anaukisidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, cotero ifenso tikayende m’moyo watsopano. Pakuti ngati ife tinakhala olumikizidwa ndi Iye m’cifanizidwe ca imfa yace, koteronso tidzakhala m’cifanizidwe ca kuuka kwace; podziwa ici, kuti umunthu wathu wakale unapacikidwa pamodzi ndi Iye, kuti thupilo la ucimo likaonongedwe, kuti ife tisakhalenso akapolo a ucimo; pakuti iye amene anafa anamasulidwa kuucimo. Koma ngati ife tinafa ndi Kristu, tikhulupirira kuti tidzakhalanso amoyo ndi Iye. Podziwa kuti Kristu anaukitsidwa kwa akufa, sadzafanso; imfa siicitanso ufumu pa Iye. Pakuti pakufa Iye, atafa ku ucimo kamodzi; ndipo pakukhala Iye wamoyo, akhala wamoyo kwa Mulungu. Cotero inunso mudziwerengere inu nokha ofafa ku ucimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Kristu Yesu.” (Aroma 6:3-11).

Onaninso pa ndime 5. “Pakuti ngati ife tinakhala olumikizidwa ndi Iye m’cifanizidwe ca imfa yace, koteronso tidzakhala m’cifanizidwe ca kuuka kwace.” Mulungu akutiuza ife kuti mphotho ya uchimo ndi imfa ndipo ali yense ali ndi machimo adzafa, adzaonongedwa, ndi kugahena. Kodi ndime ya Mateyu 5:26 ikunena kuti chidzachitike ndi chiani kwa inu ngati mwafa ndi ka tchimo kakang’ono munalandire choonadi chathunthu. Ngakhale ndi ka tchimo kakag’ono mudzaponyedwa kuchilango choopsa cha gahena.

Koma, pali Mpulumutsi wathu Yesu Kristu. Ngati kunali kulipira mphotho ya imfa yathu, sitikanapulumutsidwa; koma Mulungu anatuma Yesu ndi kulola Iye kuchotsa machimo athu onse ndi kumulanga Iye m’malo mwathu. M’malo mwa ife amene tinayenera kufa chifukwa cha machimo athu, Mulungu analola Mwana Wake kutenga machimo athu onse kudzera mu ubatizo wa Mwana Wake; Mulungu anapatsa Mwana Wake kuti apachikidwe mwankhanza ndi kukhetsa mwazi Wake wamoyo m’malo mwathu; motero Mulungu wapulumutsa ife ku machimo athu. Chikhulupiliro mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu ndi chikhulupiliro chimene chatipanga ife kuyanjana ndi Yesu Kristu.

Mphotho ya uchimo ndi imfa. Inu ndi ine tinali ndi machimo. Zotsatira zake tinayenera kupita kugahena. Chikhulupiliro chotiyanjanitsa ndi Yesu ndi kukhulupilira mu mtima mwathu kuti Yesu anachotsa machimo athu onse kudzera mu ubatizo Wake mu mtsinje wa Yordano ndi kusenza chilango cha kupachikidwa m’malo mwa ife. Choncho, imfa Yake ndi imfa yanga ndipo ubatizo Wake unali ochotsa machimo anga onse. Chikhulupiliro chotere chimatilola ife  kuyanjana ndi Kristu Yesu.Kodi Ziri Bwino Kukhulupilira Mwa Yesu Mwa Chipembedzo?


Anthu ambiri amakhulupilira Yesu mwa chipembedzo; amapita ku mpingo ndi maso a misozi kupempha chikhululukiro cha machimo ao. Iwo amalira, “Yesu, Yesu, ndi kukhulupilira kuti munandifera ine pamtanda.” Koma kodi Liwu lili lonse mu Baibulo likukupatsani chitsimikizo kuti machimo anu anakhululukidwa? Mwachidziwikire, iwo amanena kuti 1 Yohane 1:9 adzatero. 1 Yohane 1:9 akunena kuti, “Ngati tibvomereza macimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire macimo athu, ndi kutisambitsa kuticotsera cosalungama ciri conse.” Anthu amanena kuti ndimeyi imabweretsa chikhululukiro cha machimo nthawi zonse pamene iwo apemphera mapemphero akulapa. Koma chomwe ndimeyi ikunena sizakulandira chikhululukiro cha machimo pakulapa tsiku ndi tsiku, koma kulandira chipulumutso kamodzi kokha mwa kubvomereza kuti simunapulumutsidwe.

Baibulo likunena kuti, “Comweco cikhulupiliro cidza ndi mbiri, ndi mbiri idza mwa Mau a Kristu” (Aroma 10:17); “Ndipo mudzazindikira coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani” (Yohane 8:32). Choonadi ndi cholimba. Ngati Yesu akanafa pamtanda popanda kuchotsa machimo athu onse mu mtsinje wa Yordano, chikhulupiliro mwa Iye ndi cha chabe. Kuti okhulupilira apulumutsidwe ku machimo onse, munthuyo ayenera kukhulupilira ndi mtima onse mu Uthenga Wabwino wakale omwe mukupezeka ubatizo ndi mwazi wa Yesu Kristu. Kunalembedwa, “Ndipo palibe cipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo” (Macitidwe a Atumwi 4:12). Yesu Kristu anachotsa machimo athu onse ndi kukhala Mpulumutsi wathu kudzera mu ubatizo Wake. Monga dzina Lake likunenera, tinapangidwa mu chipulumutso ndi kubvomereza mwa pakamwa (Aroma 10:10). Kodi ndinu ochimwa? Kapena ndinu munthu olungama?

Kunalembedwa, “Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Kristu mudabvala Kristu” (Agalatiya 3:27). Yesu anafa pamtanda chifukwa Iye anabatizidwa. Kenako anauka kwa akufa m’masiku atatu ndi kukhala kudzanja la manja la mpando wa Mulungu. Motero Iye anakhala Mpulumutsi wa onse okhulupilira mwa Iye. Ngati Yesu sakanalandira ubatizo (madzi) kapena kukhetsa mwazi pamtanda, Iye sangakhale Mpulumutsi wathu. Pokhapo pamene takhulupilira mu Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu, tingapulumutsidwe.Ngakhale Mwana Wa Mose 


Okondedwa anzanga okhulupilira, mukumvetsera ku chinsinsi cha chipulumutso cha  madzi a ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Ili ndi dalitsodi lalikulu kumvera Mau a Mulungu. Kodi chipulumutso ndi mwa mwazi okha? Mbeu ya Abrahamu m’Chipangano Chakale ikanapulumutsidwa ndi kukhala anthu a Mulungu kudzera mu mdulidwe ndi mwazi wa mwanawankhosa wa Paskha. M’masiku a Chipangano Chatsopano, tinakhala anthu a Mulungu pokhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Chidziwitso chikuperekedwanso kwa ife kudzera mwa Mose. Mulungu anauza Mose kuti apite ku Aigupto ndi kutsogolera a Israyeli kuchoka kumaloko. Iye anauza mpongozi wake, wansembe wa Medyani, za zimenezo, ndi kuyamba ulendo wake ndi mwana wake wa mwamuna ndi mkazi wake pa bulu, Iwo anaimilira chifukwa cha usiku dzuwa litalowa. Pa nthawi imeneyo, mngelo wa Mulungu anaonekera kwa iwo ndi kuyesa kupha Mose. Mkazi wa Mose Zipora anadziwa chifukwa chache. Choncho iye anatenga mpeni wa mwara nadula khungu la mwana wake, naliponya pa mapazi a Mose, ndi kunena kuti, “Pakuti iwe ndiwe mkwati wanga wa mwazi” (Eksodo 4:25). Ndipo Ambuye analola Mose kuyenda. Mulungu anaonetsa chifuniro Chake kuti angaphe ngakhale mwana wa Mose pamene iye sanadulidwe. Kwa a Israyeli, mdulidwe unali chidziwitso cha lonjezo la Mulungu. Mulungu anati adzachotsa ali yense ngakhale mwana wa mtsogoleri, amene sanadulidwe. Choncho Mulungu anachenjeza Mose kuti asunge mwana wake. Kunalembedwa, “Koma Zipora anatenga mpeni wamwala, nadula khungu la mwana wace, naliponya pa mapazi ace; nati, pakuti iwe ndiwe mkwati wanga wamwazi. Ndipo Iye anamleka. Pamenepo anati mkaziyo, Mkwati wa mwazi iwe, chifukwa cha mdulidwe” (Eksodo 4:25-26). Baibulo likutiuza kuti Mulungu akanapha Mose chifukwa mwana wake sanadulidwe. Kupatula kuti iye anali ndani, osadulidwa ankachotsedwa pakati pa a Israyeli. Okhao a Israyeli amene anadulidwa anatenga mbali muchikondwerero ndi kudya mwanawankhosa wa Paskha.

Mtumwi Paulo anali mu Yuda. Iye anadulidwa pamene iye anali ndi masiku asanu ndi atatu akubadwa; iye analeledwa pa mapazi a Gamalieli, m’modzi mwa aphunzitsi akulu pa nthawi imeneyo; ndipo anadziwa choonadi chimene Yesu anayenera kubatizidwira mu mtsinje wa Yordano ndi kufa pamtanda. Iye ankadziwa choonadi, Uthenga Wabwino wakale omwe machimo onse anadulidwa mwachikhulupiliro chake mu ubatizo wa Yesu ndi kupachikidwa kwake; ndipo iye analalikira pa za ubatizo wa Yesu mu kalata yake ili yonse kuphatikiza buku la Aroma ndi buku la Agalatiya. 

Ndi zoona, mtumwi Paulo anakamba mobwereza za ubatizo wa Yesu, umene ndi chomaliza cha chipulumutso. Koma mwazi unali umboni omaliza wa choonadi chonse, koma mdulidwe wa uzimu oona wapezeka mwa Uthenga Wabwino wakale wa ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Iye anakamba kuti ubatizo wa Yesu unali ofunika kupanga mwazi wa Yesu kukhala wa mphamvu. Iye ananena mobwereza za mtanda. Kodi n’chifukwa chiani anachita zimenezi? Ndi chifukwa choti ubatizo ndi umboni omaliza pa chipulumutso chathu. Akanakhala kuti Yesu sanalandire chilango pamtanda pokhetsa mwazi Wake ngakhale kuti Iye anachotsa machimo athu, sitikanalandira chipulumutso cha ngwiro. Mtanda ndi mathero a ntchito yolungama ya Yesu pa chipulumutso chathu.

Ngati chikhulupiliro chabwino chokhulupilira mu ubatizo wa Yesu pamodzi ndi mtanda zikanasungidwa, Akristu a lero onse akanakhala anthu a Mulungu opanda uchimo. Koma ndi zachisoni, Akristu sadziwabe za ubatizo wa Yesu koma amakhulupilira mu mwazi okha wa Yesu ngati chipulumutso, chomwe ndi chimodzi modzi ndi chigoba chopanda kanthu mkati. Choncho amakhalabe ochimwa posatengera kuti ndi dzaka dzingati zomwe akhala kukhulupilira mwa Yesu.Umboni Wanga


Ndinali ndi dzaka makumi awiri zakubadwa pamene ndinayamba kukhulupilira mwa Yesu. Anthu akanena kuti Yesu anafera ochimwa ngati ine. Sindinkadziwa Mulungu kapena lamulo Lake. Kapena kudziwa momwe ndachimwira, koma ndinkakhalabe moyo osangalala. Koma tsiku lina ndinadwala. Ndinadwala kwambiri moti ndinkaganiza kuti nditha kufa. Ndinaganiza, “ndifa pompano. Ndikufuna kuti ndilandire chikhululukiro cha machimo ndisanafe. Anthu amanena kuti Yesu anafera anthu ochimwa.” Choncho ndinakhulupilira mwa Iye. Nthawi yoyamba ndinakhulupilira, ndinadzimva kuthokoza, koma ndinali ochimwabe chaka ndi chaka kwa dzaka khumi. Ndinakhalabe ochimwa ngakhale ndinakhulupilira mwa Yesu mosangalala.

Ngakhale ndinkaimba, “♪kulira sikudzandipulumutsa ine,” ndinkalira nthawi zonse pamene ndachimwa. “Mulungu chonde ndikhululukireni ine. Chonde ndikhululukireni pa tchimo ili. Ngati mudzakhululuka, ndidzachita bwino nthawi ina.” Pamene ndachita tchimo, ndinkatha masiku atatu kupemphera mapemphero akulapa. Sindinkadya chifukwa cha mlandu wachikumbumtima changa. Ndinkadzitsekera ndeka ndikulira kwa Mulungu kuti andikhululukire. Ndikalira ndi mtima wanga, ndinkamva bwino komanso ndinkafa ngati ndingamve Mau a Mulungu. “ndatsuka machimo anga moyera. Aleluya!” ndinkachoka momwe ndinabisala ndikuyamba kutumikira ena mwa mphamvu. Ndipo mwakanthawi, kupatula ine mwini, sindinkadzithandiza koma kuchimwanso.

Pachiyambi, zinali zabwino kukhulupilira mwa Yesu, koma pamene nthawi inali kupita, machimo anga anali kuchulukira. Machimo ndi mulu monga uja wa manyuwa ndi zonyansa. Dzaka khumi za moyo wanga mwa Kristu zinachulukitsa machimo mu mtima mwanga kwambiri kuposa masiku amene ndinali osakhulupilira. Ndinakhala ochimwa oopsa. Ndinalilira moyo wanga wa chipembedzo, “kodi n’chufukwa chiani ndinakhala okhulupilira ndidakali mwana? Ndikanayembekeza mpaka nditafika dzaka 80, ndisanafe. Ndikudwala ndipo ndatopa ndikupemphera mapemphero akulapa tsiku ndi tsiku. Ndikudziwa kuti ndi yenera kukhala molingana ndi chifuniro cha Mulungu, koma sizophweka. Ndikudwala zimenezi.”

Ndinkayang’ana ndikuyang’ana Mulungu. Choncho ndinaphunzira maphunziro azaumulungu. Zodabwitsa, maphunziro azaumulungu anapanga chikhulupiliro changa kukhala chopanda kanthu motheratu. Ndisanayambe maphunziro azaumulungu, ndinaganiza, “sindizagona pakama wofunda monga woyera mtima Damiani. Ndidzatandiza obvutika. Sindidzakhala bwino koma ndidzatandiza anthu awa osowa.” Ndinali ndi maganizo otere pamene ndinkawerenga zamoyo wa oyera mtima. Ndinkakhala moyo oyesetsa popemphera mwa mabondo anga pansi polimba kwa maola angapo. Izo zinkaoneka monga zikugwira ntchito ndikundipanga ine kumva bwino. 

Koma patatha dzaka khumi, sindinathenso kuimilira. Choncho ndinalira. “Mulungu, O Mulungu, chonde ndi pulumutseni. Ndimakhulupiliradi mwa Inu, ndipo ndidzapitiriza kukhulupilirabe mwa Inu ngakhale wina andiopseze kuti ndisakhulipilire mwa Inu ndi mpeni pa khosi panga. Koma kodi n’chifukwa chiani mtima wanga uli opanda kanthu ndi ozunzika? Ndisanakhulupilire mwa Yesu ndinalibe machimo ambiri, koma n’chifukwa chiani ndakhala ochimwa kwambiri?” Tsopano nditha kunena kuti chinali chifukwa chakuti sindinadziwe choonadi komanso sindinalandire chikhululukiro cha machimo. Koma pa nthawi imeneyo ndinali muzowawa.

Kodi ndingauze bwanji ena kuti akhulupilire mwa Yesu kapena kuti alandire chikhululukiro cha machimo pamene ndili odzadza ndi machimo? Choncho ndinafuula kunena kuti, “okodedwa Mulungu, pompano ndi tsiriza maphunziro anga. Ndipo ndidzadzozedwa ngati mbusa, koma kodi ndingauze bwanji ochimwa kuti alandire chikhululukiro cha machimo pamene ndidakali ochimwa?” Mukalata ya mtumwi Paulo, iye anati, “Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Kristu, siali wace wa Kristu.” Sindinkadzimva Mzimu mwa ine. Ndinkaganiza kuti mwa chidziwikire ndinali nao, koma n’chifukwa chiani Iye anasowa posachedwapo? Kodi Iye ali pamalonda oyenda yenda? Kodi chikuchitika ndi chiani, Mulungu? Mwazoona ndinkakhala mu mphamvu yoti ndinapulumutsidwa mwa Yesu mwa njira inayake. Ndinali mu zowawa. Ndinalila kwambiri. Sindingakuuzeni zonse.

Mulungu analonjeza kuti Iye adzazibvumbulutsa Yekha kwa iwo amene akufuna funa Iye. Choncho Mulungu anakumana ndi ine. Ndakhala ochimwa ngakhale ndinkakhulupilira mwa Yesu bwino bwino kwa dzaka khumi. Koma, pamene ndinapeza chinsinsi cha ubatizo wa Yesu, mdulidwe wa uzimu m’Chipangano Chatsopano, mabvuto anga onse anatha. Machimo anga onse anasowa ndipo mtima wanga unayeretsedwa mbuu ngati matalala.

Pamene mwakhulupilira mu Uthenga Wabwino wakale omwe muli ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, ndi chachidziwikire kuti machimo anu adzasowa kamodzi kokha. Ziribe kanthu kuti ndinu operewera motani, simudzakhalabe mu machimo. Mudzalalikira Uthenga Wabwinowo kwa anthu komanso kwa iwo amene adzalandire Uthengawu adzaladira chikhululukiro cha machimo ndi kutamanda Mulungu ndi ‘Aleluya.’ Ndikuyamikira iwo a inu omwe machimo anu akhululukidwa. Ndikutamanda Yesu amene anatipulumutsa ku machimo athu onse. Talandira chikhululukiro cha machimo mwa chimwemwe.

Sitingaonetse chimwemwe chathu chonse cha chikhululukiro cha machimo. Choncho, tiyeni tiyimbe nyimbo yomwe ikuti, “♪ Yesu, dzina, lomwe sindingalikambe mokwanira. ♪ Chinsinsi mu dzina, lalikulu kwambiri kugawana, lakhala chinsinsi. ♪ Anthu anakana dzina ngati amisili. ♪ Koma dzina lomwe lakhala pa mtima wanga ndi mwala wamtengo wapatali.”Ubatizo Ndi Mwazi Wa Yesu Omwe Unapulumutsa Ochimwa Mokwanira


Yesu anatsuka ndi kupulumutsa ife mokwanira kudzera mu mdulidwe wa uzimu, ubatizo Wake. Iye anatipanga ife anthu a Mulungu. Kudzera mu chitetezero cha Yesu, Mulungu wakhala Mulungu wa Obadwa mwatsopano. Monga Iye analonjezera m’Chipangano Chakale, Yesu analandira Ubatizo, kunyamula machimo adziko lapansi kupita nao pamtanda, ndikufa kukhala Mpulumutsi wa ochimwa. Iye anakhala Mulungu Mpulumutsi wa mtundu onse wa anthu. 

Machimo amadzetsa chilango. Koma Yesu anabatizidwa ndi kupachikidwa kuti apulumutse ife; ndipo mwa kukhetsa mwazi Wake wamtengo wapatali, Iye anapulumutsa ine ndi inu; Iye anaukanso kwa akufa mwa masiku atatu. Mulungu Atate anaukitsa Iye kwa akufa. Moyo wa Yesu Kristu ndi moyo wathu, komanso umboni woti takhala ana a Mulungu. Ubatizo wa Yesu Kristu unachotsa machimo athu onse. Mwazi wa Yesu Kristu ndi chidziwitso choti Iye anasenza chilango cha ife.

Kodi muli ndi umboni mu mtima mwanu wa ubatizo ndi mwazi wa Yesu? Kodi tinalandira chikhululukiro cha machimo mwa mwazi okha wa Yesu Kristu? Ai. Chipulumutso chakwaniritsidwa mwa ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Yesu anakwaniritsa chipulumutso.Kodi Mpatuko Ndi Chiani?


Kodi ndinu ochimwabe pamene mwakhulupilira mwa Yesu nthawi zonse? Ngati izi ziri chonchi, chikhulupiliro chanu ndi cha mpatuko. Mpatuko ndi chikhulupiliro chimene ndi chosiyana ndi zimene Mulungu akunena. Tito 3:10-11 akutichenjeza zampatuko; “Munthu wopatukira chikhulupiriro, utamcenjeza kamodzi ndi kawiri, umkanize, podziwa kuti wotereyo wasandulika konse, nacimwa, nakhala wodzitsutsa yekha.” Iwo amene ali odzitsutsa okha, iwo amene amadzicha okha ngati ochimwa amanena kuti, “Mulungu, ndine ochimwa posatengera zomwe ena akunena,” ndi ampatuko. Mulungu akuuza iwo, “chabwino, ndinu ochimwa. Sindinu ana anga. Ndinu ampatuko. Muli ndi moto osazimitsika ukukuyembekezerani.” Iwo amene akhulupilira mwa Yesu koma akukanabe kulandira Uthenga Wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi odzitsutsa okha ochimwa ndi ampatuko pamaso pa Mulungu.Kodi Okhulupilira Oonadi Ndindani?


Ali yense amene akhulupilira mu Uthenga Wabwino wakale, omwe ndi, ubatizo ndi mwazi wa Yesu, ndi munthu olungama popanda kuchotsera. Kodi tingakhale bwanji ochimwabe pamene taika chikhulupiliro chathu mwa Yesu? Ochimwa sangalowe kumwamba. Iwo amene akhala olungama pokhulupilira mwa Yesu ali ndi umboni mwa iwo omwe ndi ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Ntchito ya chipulumutso ndi yomwe Yesu anachita pa dziko lino. Iwo amene sakhulupilira mu Uthenga Wabwino wakale omwe ukunena kuti Yesu analandira ubatizo chifukwa cha chipulumutso chathu ndo kuchotsa machimo athu onse adzachotsedwa ndi kukanidwa ndi Mulungu. Uthenga Wabwino wakale umanena kuti Yesu anadza pa dziko lino; iye anadulidwa mu uzimu; Iye anatenga chilango pamtanda kupulumutsa ife kuchiweruzo; anaukanso kwa akufa ndi kukhala Mulungu wathu wa moyo. Ali yense okhulupilira mu Uthenga Wabwino wakale uwu wapulumutsidwa. Ichi ndi chipulumutso mwa madzi, mwazi ndi Mzimu (1 Yohane 5:4-8). Ubatizo, mwazi ndi Mzimu ndi umboni kuti Yesu anapulumutsa ife ku machimo a dziko. Ndi umboni wa chipulumutso chomwe Mwana Mulungu anakwaniritsa kwa ife.

Okodedwa anzanga okhulupilira, kodi mukubvomera tsopano Uthenga wabwino wakale? Kodi mukubvomera kuti chipulumutso sichinakwaniritsidwe mwa mwazi okha wa Yesu, koma mwa madzi a ubatizo, ndi mwazi, ndi Mzimu? Mulungu anachotsa machimo a ochimwa onse kudzera mu ubatizo wa Yesu. Iye anachita mdulidwe wa uzimu pa ife. Umu ndi m’mene anachotsera machimo a dziko kwa ife. Ndipo Iye anapulumutsa ife kotheratu popereka mphotho ndi mwazi Wake pamtanda. Iye sanachotse machimo athu onse okha, koma machimonso a dziko, kuyambira machimo a Adamu kufikira machimo a munthu omaliza pa dziko lapansi. Ali yense amene wakhulupilira zomwe yesu anachita pa dziko lino kudzera mwa madzi, mwazi, ndi Mzimu walandira chipulumutso ku machimo onse. Ichi ndi choonadi komanso nzeru ya Uthenga Wabwino wakale. 

Yesu anachotsa machimo onse a dziko mwa ubatizo Wake kuti anthu apulumutsidwe. Tsopano nzosatheka kuti ife tikhale ndi tchimo pamene takhulupilira mwa Yesu. Yesu anatidzutsa ife mwa akufa. Yesu anatsitsimutsa mizimu yosowa yomwe inasowa chifukwa cha Satana Mdierekezi. Iye anapeza mizimu yosowa. Tinapezeka mwa Yesu ndi kulandira chikhululukiro cha machimo kudzera mwa Yesu Kristu, mwa madzi, mwazi, ndi Mzimu.

Kodi inu mukukhulupiliranso zimenezi? Ndikufuna ndikuuzeni kuti chipulumutso simwa mwazi okha koma ndi mwa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pamtanda. Ndikudziwa kuti anthu amene akunena kuti anapulumutsidwa kudzera mwa mwazi okha wa Yesu adakali olemedwa ndi machimo mu mitima yao. Tonse tinkakhulupilira kuti tinapulumutsidwa mwa mwazi okha wa Yesu. Koma izi sizoona. Timalandira chipulumutso chotipanga ife kubadwa mwatsopano pokhulupilira mwa Yesu Kristu, amene anadza mwa madzi, mwazi ndi Mzimu. 

Yesu Kristu anatipanga ife opanda tchimo pochotsa machimo athu onse. Kodi chipulumutso chathu chili mwa mwazi okha wa Yesu? Ai. Ndi mwa madzi (ubatizo wa Yesu), mwazi (imfa Yake pamtanda) komanso kuuka Kwake. Kutipulumutsa ife mwa madzi ndi mwazi kunali mbali ya chikonzero cha Mulungu chomwe Iye anali nacho lisanakhazikike dziko lapansi. Izi zonse zinali ntchito yachipulumutso imene Mulungu anachita. Kubadwa mwatsopano ndikukhala omasuka ku machimo kunakwaniritsidwa mwa chikhulupiliro chathu chokha mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu (1 Yohane 5:5-10). Uthenga Wabwino wakale omwe Yesu anakamba unapangidwa ndi ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pamtanda. 

Yamikani Ambuye! Aleluya!