Sermons

【3-12】 Ubwenzi Pakati Pa Utumiki Wa Yohane Mbatizi Ndi Uthenga Wabwino Wa Chitetezero Cha Machimo<Mateyu 21:32>

“Popeza Yohane anadza kwa inu mn’jira ya cilungamo, ndipo simunamvera iye; koma amisonkho ndi akhazi aciwerewere anam’mvera iye; ndipo inu, m’mene munaciona, simunalapa pambuyo pace, kuti munvere iye.”Yohane Mbatizi Anatumizidwa Ndi Mulungu


Baibulo limachitira umboni za Yohane Mbatizi mu Yohane 1:6-7, “kunali munthu, wotumidwa ndi Mulungu, dzina lace ndi Yohane. Iyeyu anadza mwa umboni kudzacita umboni za kuunikaku, kuti onse akakhulupirire mwa iye.” Monga kwalembedwa apa, Yohane Mbatizi “anadza chifukwa cha umboni, kuchitira umboni za kuunika, kuti onse kudzera mwa iye akhulupilire.” Umboni omwe Yohane Mbatizi anachitira unali wonena kuti yesu anasenza machimo a dziko, ndipo ngati iye sakanapereka umboni umenewu wa Uthenga Wabwino wa Yesu wa chitetezero cha machimo, kukanakhala kosatheka kwa ali yense kukhulupilira mwa Yesu ndipo, ngakhale m’modzi akanachita, zonse zikanakhala mwa chabe. Mukulankhula za Yohane Mbatizi, mtumwi Yohane akufotokoza Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo pamenepa, monga m’mene zimakhalira kwa ali yense amene wapeza Yesu ife tisanamupeze kuti ifenso tadziwa ndi kukhulupilira mwa Iye. Kodi Yohane Mbatizi Anali Ndani?


Kunalembedwa mu Luka 1:76-77: “Eya, ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa mneneri wa wamkulukulu: pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njiran zace; wapatsa anthu ace adziwitse cipulumutso, ndi makhululukidwe a macimo ao.” Mneneri wa wamkulukulu apa ndi osaposa Yohane Mbatizi, oimilira wa mtundu onse wa anthu amene, mwakupatsira machimo onse a anthu a Ambuye kwa Yesu kudzera mu ubatizo, kunadziwika kwa okhulupilira onse ambuye kuti iwo apulumutsidwa ku chiweruzo ndi kulandira chikhululukiro cha machimo. Baibulo limafotokozanso chifukwa chimene Yohane Mbatizi anatumizidwa pa dziko lino monga oimilira wa mtundu wa anthu onse kuti apatsire machimo onse a anthu a Mulungu kwa Yesu, ndipo Luka 1:78 akuchitira umboni kuti chifukwa chimenechi ndi “chifundo cha Mulungu wathu.” Mwa umboni wa Yohane Mbatizi koma anthu onse anadziwa chipulumutso cha Ambuye, monga kunalembedwa, “Cifukwa ca mtima wacifundo wa Mulungu wathu. M’menemo mbanda kuca wa kumwamba udzaticera ife” (Luka 1:78). 

Yesu ndi chitsimikizo chotsimikizira ife kuti chitetezero chinachitika ku machimo athu onse. Kodi ndani amene wa tsogolera ife kunjira ya amtendere mu dziko lino? Ndi Yesu. Koma chifukwa Yohane Mbatizi anapatsira machimo athu onse kwa Yesu kudzera mu ubatizo Wake ndi kutsogolera ife ku Uthenga Wabwino wa Ambuye wa chitetezero cha machimo, popanda umboni wake palibe angapeze chipulumutso mwa kumvetsetsa kwake. Tiyeni tione Mau mwatsatanetsatane kuti tione Yohane Mbatizi anali ndani. Kunalembedwa  mu Luka 1:1-14: “POPEZA ambiri anayesa kulongosola nkhani ya zinthu zinacitika pakati pa ife, monga anazipereka kwa ife iwo amene anakhala mboni ndi atumiki a mau, kuyambira paciyambi, ndinayesa nkokoma ineso, amene ndinalondalonda mosamalitsa zinthu zonse kuyambira paciyambi, kulembera kwa iwe tsatane tsatane, Teofilo wabwinotu iwe; kuti udziwitse zoona zace za mau amene unaphunzira. Masiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kunali munthu wansembe, dzina lace Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya; ndi mkazi wace wa ana akazi a pfuko la Aroni, dzina lace Elisabeti. Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m’malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osacimwa. Ndipo analibe mwana, popeza Elisabeti anali wouma, ndipo onse awiri anakalamba. Ndipo panali, pakucita iye ntchito yakupereka nsembe m’dongosolo la gulu lace, pamaso pa Mulungu, monga mwa macitidwe a kupereka nsembe, adamgwera maere akufukiza zonunkhikira polowa iye m’Kacisi wa Ambuye. Ndipo khamu lonse la anthu linali kupemphera kunja nthawi ya zonunkhira.Ndipo anamuonekera iye mngelo wa Ambuye, naimirira ku dzanja lamanja la guwa la nsembe la zonunkhira. Ndipo Zakariya anadabwa pamene anamuona, ndipo mantha anamgwira.Koma mngelo anati kwa iye, Usaope Zakariya, cifukwa kuti lamveka pemphero lako, ndipo mkazi wako adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamucha dzina lace Yohane. Ndipo udzakhala nako kukondwera ndi msangalalo; ndipo anthu ambiri adzakondwera pa kubadwa kwace.” 

Uthenga Wabwino wa Luka unayamba mwa kunena kuti, Luka, anazindikira zochitika za Yesu mwatsatanetsatane kuchokera kuchiyambi, ndipo iye anayamba kufotokoza mwa kuyambira mbadwo wa Yohane Mbatizi choyamba. Tiyeni tionenso poyamg’ana pa mbadwo wa Yohane Mbatizi apa ndi kuona kubadwa kwake ndi utumiki wake mwatsatanetsatane.

Luka, ophunzira wa Yesu, analalikira Uthenga Wabwino kwa olemekezeka wa a mitundu ina. Koma munthu ameneyu sankadziwa malemba a Mau a Mulungu, ndipo kenako kunali kofunika kuti Luka afotokoze Mau kwa iwo mwatsatanetsatane, ndipo ichi ndi chifukwa iye anayamba nkhani yake ndi mbadwo wa Yohane Mbatizi.

Kunalembedwa, “Masiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kunali munthu wansembe, dzina lace Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya; ndi mkazi wace wa ana akazi a pfuko la Aroni, dzina lace Elisabeti. Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m’malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osacimwa. Ndipo analibe mwana, popeza Elisabeti anali wouma, ndipo onse awiri anakalamba.Ndipo panali, pakucita iye ntchito yakupereka nsembe m’dongosolo la gulu lace, pamaso pa Mulungu, monga mwa macitidwe a kupereka nsembe, adamgwera maere akufukiza zonunkhikira polowa iye m’Kacisi wa Ambuye.”

Apa tikuona Zakariya wansembe anali kutumikira unsembe wake mwa dongosolo la gulu lake. Ndipo Luka anachitira umboni oyera kuti mkazi wa Zakariya Elisabeti anali wafuko la Aroni. Kenako tsopano, tiyenera kufufuza apa za mbadwo wa Zakariya—ndiye kuti ndi nyumba iti ya Alevi yomwe iye anali kuchokera. 

Luka 1:8 akunena kuti, “Ndipo panali, pakucita iye [Zakariya] ntchito yakupereka nsembe m’dongosolo la gulu lace.”  Mu ndime imeneyi tikuona Luka ali kuchitira umboni kuti Zakariya anali wa m’nyumba ya Aroni mkulu wansembe, chifukwa iye anali wa “gulu la Abiya,” m’modzi mwa zidzukulu za Aroni. Ndipo keneka anakamba za mbadwo wa Yohane mbatizi ngati wafuko la Aroni mkulu wansembe, Luka ananenso kuti mkazi wa Zakariya Elisabeti anali wafuko la Aroninso. 

Yohane mbatizi anabadwa kuchokera kwa Zakariya atate wake. Tiyeni tsopano tibwerere ku mbadwo wa Zakariya wansembe. Pamene tikubvundukula 1 Mbiri 24:10 “wacisanu ndi ciwiri Hakozi, wacisanu ndi citatu Abiya.” Mulungu anadzutsa Mose ngati oimilira Wake, ndipo iye anadzodza Aroni, mbale wa Mose, ngati mkulu wansembe kuti atumikire Mulungu pamaso pa anthu a Israyeli. Ana amuna a Aroni awiri anaphedwa pamene ankapereka zofukiza kwa Mulungu ndi moto onyoza omwe unali osayeretsedwa. Iwo atafa, panali a nsembe awiri otchedwa Eleazara ndi Itamara, omwe onse anali ana Aroni. Kenako Mulungu anapanga afuko la Aroni kutumikira nsembe zonse ndi kutumikira Ambuye mu kachisi. Nambala ya mbeu ya Aroni inakula mwa kupita kwa nthawi. Choncho, m’masiku a Davide, iye anafunika kuika mudongosolo unsembe molingana ndi magulu a zidzukulu 24 za Aroni. Mwanjira ina, Davide anagawa a nsembe m’magulu osinthana mu kutumikira nsembe, ndipo iyi ndi “dongosolo la magulu” lomwe latchulidwa mu Luka 1, omwe akunena kuti Zakariya anapita mkachisi ya Ambuye kuti atumikire iye mu dongosolo la gulu lake pamene maere ake anamgwera.

 Pamene Davide anabwezeretsa ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe kukachisi, iye anayeneranso kukonza dongosolo lomwe ansembe ankatumikira nsembe. Davide anabwezeretsa ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe chifukwa a Israyeli anapembedza mafano kwambiri mu nthawi ya masiku a Saulo, ndipo iye anapatsa ntchito ansembe onse afuko la Aroni kupereka machimo a ana a Israyeli pa nyama za nsembe ku chitetezero cha machimo ndi chipulumutso. Ndipo chifukwa panali afuko a mbiri a Aroni, Davide anakhazikitsa dongosolo lomwe ansembe ankasinthana kulowa mukachisi ndi kutumikira Ambuye malingana ndi dongosololi. 

Ndi mucholozera kudongosololi lomwe 1 Mbiri 24:10 akunena, monga momwe tawerengera, “wacisanu ndi citatu Abiya”; komanso Luka 1:5, omwe akunena kuti, Luka 1:5 “Kunali... wansembe, dzina lace Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya,” kutsimikiza kuti Zakariya anali wafuko wa nsembe wa gulu la Abiya, m’modzi mwa zidzukulu za Aroni. Moonekeratu, ndiye kuti atate ake a Yohane Mbatizi anali wa nsembe wa gulu la Abiya komanso wa fuko la Aroni mkulu wansembe. Kuonjezerapo, Baibulo likunenanso apa kuti Elisabeti anali wafukonso la Aroni (Luka 1:5). Choncho, onse amayi ndi atate a Yohane Mbatizi anali a fuko la Aroni mkulu wansembe. Kunali kofunika kuti Luka afotokoze izi momveka bwino kwa Teofilo choyamba asanafotokoze kwa iye kuti Yohane Mbatizi anapatsira machimo onse kwa Yesu. Tsopano, tiyeni tibwerere ku Mau a malemba kuti tione pomwe akunena kuti afuko la Aroni anatumikira ngati mkulu wansembe.Yohane Mbatizi Anabadwa Mu Nyumba Ya Mkulu Wansembe


Choyamba, mbeu ya Aroni inatenga utumiki wa unsembe wa tsiku la chitetezero. Kunalembedwa mu Levitiko 16:30-34 “popeza tsikuli adzacitira inu cotetezera, kukuyeretsani; adzakuyeretsani, kukucotserani zoipa zanu zonse pamaso pa Yehova. Lkhala kwa inu sabata lakupumula, kuti mudzicepetse; ndilo lemba losatha. Ndipo wansembe, amene anamdzoza ndi kumdzaza zanja lace acite nchito ya nsembe m’malo mwa atate wace, acite cotetezera, atabvala zobvala zabafuta, zobvala zopatulikazo. Ndipo acite cotetezera malo opatulikatu, natetezere cihema cokomanako, ndi guwa la nsembe; momwemo atetezerenso ansembe, ndi anthu onse a msonkhanowo. Ndipo ici cikhale kwa inu lemba losatha, kucita cotetezera ana a Israyeli, cifukwa ca zocimwa zao zonse, kamodzi caka cimodzi. Ndipo anacita monga Yehova adauza Mose.” 

Mu Numeri 20:28-29, Baibulo likunena kuti, “Ndipo Mose anabvula Aroni zobvala zace, nabveka Eleazara mwana wace; ndipo Aroni anafa pomwepo pamwamba pa phiri. Pamenepo Mose ndi Eleazara anatsika m’phirimo. Pamene khamu lonse linaona kuti Aroni adamwalira, anamlira Aroni masiku makumi atatu, ndiyo mbumba yonse ya Israyeli.” Monga m’mene tikuonera apa, Mulungu anapatsa ofesi ya mkulu wansembe kwa Aroni ndipo ofesi imeneyi inatsikira pa ana ake, ndipo lamulo limeneli linakhala losasinthidwa kwamuyaya (Levitiko 16:33-34). Mwa ana onse a Israyeli, ndi Aroni ndi ana ake amuna amene anapatsidwa ntchito ya unsembe kuti atumikire Mulungu. Umo ndi m’mene Aroni ndi ana ake amuna anakhalira nyumba ya mkulu wansembe omwe ankatumikira kubweretsa chikhululukiro cha machimo ku anthu a Israyeli.

Kunalembedwa mu Eksodo 28:1-2: “Ndipo akuyandikire Aroni mbale wako, ndi ana ace amuna pamodzi naye, mwa ana a Israyeli, kuti andicitire Ine ntchito ya nsembe, ndiwo Aroni, Nadabu, ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni. Ndipo usokere Aroni mbale wako zobvala zopatulika, zikhale zaulemelero ndi zokoma.”

Mulungu ananenso mu Eksodo 29:1-9: “Ici ndico uwacitire kuwapatula, andicitire nchito ya nsembe: tenga ng’ombe yamphongo, ndi nkhosa ziwiri zamphongo zangwiro, ndi mkate wopanda cotupitsa, ndi timitanda topanda cotupitsa tosanganiza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda cotupitsa, todzodza ndi mafuta; utipange ndi ufa wosalala watirigu. Ndipo uziike mu mtanga umodzi, ndi kubwera nazo mumtanga, pamodzi ndi ng’ombe yamphongo, ndi nkhosa ziwiri zamphongo. Ndipo ubere nao Aroni ndi ana ace amuna ku khomo la cihema cokumanako, ndi kuwasambitsa m’madzi. Pamenepo utenge zobvalazo ndi kubveka Aroni maraya am’kati, ndi mwinjiro wa efodi, ndi efodi, ndi capacifuwa, ndi kummangira m’cuuno ndi mpango wa efodi woluka mwanzeru; ndipo uike nduwira pamutu pace, ndi kuika korona wopatulika panduwirapo. Pamenepo utenge mafuta odzodza nao nuwatsanulire pamutu pace, ndi kumdzoza. Ndipo ubwere nao ana ace amuna ndi kuwabveka maraya am’kati. Uwamangirenso Aroni ndi ana ace amuna mipango m’cuuno mwao, nuwamangire akapa pamutu pao; ndipo akhale ansembe mwa lemba losatha; nudzaze dzanja la Aroni ndi ana ace amuna.”

Tsopano, palibe chokaikitsa kuti Mulungu anagwiritsa ntchito nyumba ya Aroni, mbale wa Mose, ngati nyumba ya mkulu wansembe oimilira anthu a Israyeli. Palibe angakangane ndi izi. Ndi mwa lamulo la Mulungu kuti nyumba ya Aroni inyamule ofesi imeneyi ya mkulu wansembe. Osati ali yense akananyamula ofesiyi ya mkulu wansembe, koma yekhayo wa nyumba ya Aroni akanatha kutumikira ngati mkulu wa nsembe kulowa m’malo patulikitsitsa akachisi ndi kuchotsa machimo onse a chaka a anthu onse a Israyeli kamodzi kokha. Choncho Mulungu anauza Mose kuti asankhe mbale wake Aroni ku ukulu wansembe (Eksodo 29:1), ndipo anauzanso Mose kuti apange mkanjo wa mkulu wansembe anamuonetsa iye ndi kumubvalika mkanjowo pa mbale wake Aroni. 

Izi zikutanthauza kuti kunaikidwa ndi Mulungu mwini kwa Aroni kuti akhale mkulu wansembe komanso kwa ana ake amuna komanso afuko lake kukhala ansembe. Mulungu ananena kuti ofesi ya mkulu wansembe iyenera kugona pa ana ake amuna a Aroni komanso afuko lake; afuko la Aroni choncho anayenera kutumikira ngati akulu ansembe mpaka kutha kwa nthawi ya Chipangano Chakale kufikira nthawi ya Chipangano Chatsopano ndi kubwera kwa Yesu; ndipo ichi chinali chilamulo chosatha cha chipulumutso chinakhazikitsidwa ndi Mulungu kuchitetezero cha machimo.

Ichi n’chifukwa chake Luka ananena kuti Zakariya anali wa nyumba ya Aroni mkulu wansembe, kufotokoza kuti Yohane Mbatizi anali mkulu wansembe omaliza wa Chipangano Chakale. Pamene Yohane Mbatizi anapatsila machimo onse a dziko pa Yesu m’malo mwa mtundu onse wa anthu, pangano m’Chipangano Chakale linatha, ndipo kuyambira nthawi ya Yesu, nthawi ya chisomo. Umu ndi m’mene Mulungu anakwaniritsira mbiri ya mtundu wa anthu mu nyengo ziwiri zosiyana.Yohane Mbatizi Anabatiza Yesu 


Timatcha Yohane “Yohane Mbatizi” chifukwa iye anabatiza Yesu. Nanga, kodi, “ubatizo” ukutanthauza chiani mu Baibulo? Mau oti “ubatizo” ndi (baptisma) mu chi Greek, omwe akutanthauza kumiza, kutsuka, kupereka pa, kukwirira kapena kusamutsa. 

Monga tatchulira, ubatizo ukutanthauza kupereka pa kapena kusamutsa. Monga Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi, machimo onse adziko anaperekedwa pa Yesu; motero polandira machimo onse a ochimwa ali yense mdziko lino, Yesu kenako anaphedwa m’malo mwathu kuti apereke mphotho ya machimo athu; iye anauka kwa akufa kachiwiri; ndipo iye anakhala Mpulumutsi wa onse amene akhulupilira mu choonadichi. Ambuye anabatizidwa kusenza machimo athu m’malo mwathu ndipo Iye anapachikidwa mpaka kufa m’malo mwathu. Ndi chifukwa cha kuti mphotho ya uchimo ndi imfa.

Monga tanenera kale, Mau akuti, “ubatizo” akutanthauzanso “kutsuka.” Izi, zikutanthauza kuti Yesu analandira ubatizo wa chikhululukiro cha machimo kuchokera kwa Yohane Mbatizi mu mtsinje wa Yordano, Iye analandira machimo athu onse ndi kufafaniza machimo onse a dziko lapansi. Chifukwa chakuti machimo onse a mtundu wa anthu anaperekedwa pa thupi la Yesu kudzera mu ubatizo omwe analandira kwa Yohane Mbatizi, ndipo Yesu anachita chitetezero cha machimo onse adziko ndi thupi lake, tinapulumutsidwa mwa kukhulupilira mu choonadi chimenechi. Pamene tikuyang’ana mwatsatanetsatane pa ubatizo wa Yesu ndi tanthauzo lake, tikuona kuti pali matanthauzo anai: “kutsuka,” “kupatsira pa,” “kusamutsa,” komanso “kukwirira.”  Mu nthawi ya Chipangano Chakale, pamene anthu a Israyeli ankafuna chikhululukiro cha machimo ao, ankabweretsa nyama zopanda chirema za nsembe mwa kufuna kwa Mulungu, monga mbuzi, mwanawankhosa, ng’ombe ya mphongo, kapena nkhunda, ndipo ankaika manja ao pamutu pa nyama za nsembe kuti apatsire machimo ao paizo. Mwambo umenewu ukunyamula chofunika chofanana monga ubatizo omwe Yesu analandira nthawi ya Chipangano Chatsopano. M’Chipangano Chakale, anthu a Israyeli anapereka machimo ao kwa mbuzi poika manja ao pamutu pake, ndipo mbuziyi, popeza motero yalandira machimo a Israyeli, inkaphedwa m’malo mwao ndi kupanga chitetezero cha machimo ao. Momwemonso, Yesu naye analandira machimo a dziko mwa kubatizidwa ndi Yohane Mbatizi (oimilira mtundu onse wa anthu); Iye anakhetsa mwazi Wake mpaka kufa kuti apange chitetezero cha machimo athu onse; Iye anaukanso kwa akufa; ndipo Iye motero anapulumutsa okhulupilira ake onse. M’Chipangano Chakale, Aroni mkulu wansembe ankaika (kusamutsa) machimo a Israyeli pamutu pa mbuzi mwa kuika manja ake monga oimilira wao, kudula khosi ndi kuchotsa mwazi wake, kuika mwazi pa guwa la nsembe, ndi kupereka nsembeyo kwa Mulungu m’malo mwa anthu a Israyeli. M’Chipangano Chatsopano, Yohane Mbatizi anali oimilira mtundu onse wa anthu.Wamkulu Pakati Pa Obadwa Mwa Akazi


Pamene tibvundukula Mateyu 11:11, tikuona Yesu mwini akuchitira umboni, “Sanauke wakubadwa mwa akazi munthu wamkuru woposa Yohane Mbatizi.” Tanthauzoli ndi lomveka: Yohane Mbatizi anali okwanira kwa thunthu kukhala mkulu wansembe wa mtundu onse wa anthu. Inali ntchito yake ngati mkulu wansembe omaliza wa Chipangano Chakale amene iye anabatiza Yesu. Ngati Aroni anali mkulu wansembe wa anthu onse a Israyeli, ndiye kuti Yohane Mbatizi anali mkulu wansembe wa mtundu onse wa anthu, ndipo malingana ndi lamulo lasatha la unsembe lokhazikitsidwa nd Mulungu, iye anapatsira machimo onse a dziko pa Yesu kamodzi kokha mwa kubatiza Iye. Atate ake, Zakariya anali wa fuko la Aroni, monga m’mene amai ake Elisabeti analinso wa mnyumba ya Aroni, ndipo chifukwa afuko la Aroni okha akanatha kukwaniritsa ukulu wa unsembe, Yohane Mbatizi anali ndi zoyenera zonse kutenga ofesi ya mkulu wansembe. Kodi Abiya Ndindani?


Mbiri oyamba 24 akufotokoza dongosolo lomwe afuko a Aroni ankatumikira monga ansembe kupereka nsembe kwa Mulungu, ndipo Abiya watchulidwapo apa ngati wa dongosolo lachisanu ndi chitatu. Pamene tibvundukula Luka 1:9 mu Chipangano Chatsopano, tikuona kuti wansembe ankasankidwa m’njira yofanana ndi Chipangano Chakale “monga mwa mwambo wa unsembe,” ndipo iye osankidwayo ankatenga mpando wamkulu wa nsembe ndi kukwaniritsa ntchito yake. Mwambo umenewu wakhala ukupitilira kwa mibadwo yambiri, mpaka pamapeto pake unapeza Zakariya, bambo wake wa Yohane Mbatizi.

Atate ake a Yohane Mbatizi, Zakariya, anali mkulu wansembe obadwa ngati wa fuko la Aroni ochokera ku dongosolo la Abiya, ndipo kutsatira mbadwowu, Yohane Mbatizi anali mkulu wansembe komanso oimilira wa mtundu onse wa anthu. 

Polemba zofanana, mwana wa nkango angabadwe ku nkango okha. Chimodzi modzinso, Yohane Mbatizi anabadwa kuchokera kwa mkulu wansembe Aroni, ndipo ngati mkulu wansembe omaliza amene anakwaniritsa uneneri wa Mau a Mulungu achipulumutso, iye anagwira ntchito ya mlato wolumikiza Chipangano Chakale ku Chipangano Chatsopano. Kutsimikiza izi, Yesu mwini anati Yohane Mbatizi anali wamkuru mwa obadwa mwa akazi. Izi zinasimikizika mu Mateyu 11:11-13. Yesu mwini anapereka umboni wa Yohane Mbatizi ndipo ananena kuti iye anali Eliya olonjezedwa kuti atumizidwe m’Chipangano Chakale (11:13-15), ndipo lonjezo limeneli linalembedwa mu Malaki 3:4.Tiyeni Timve Umboni Wa Atumwi Pa Za Ubatizo Wa Yesu


Ubatizo wa Yesu ndi njira yomwe Ambuye wathu ana senzera machimo onse a dziko lapansi ndi kupanga chitetezero cha machimowo ubatizo Wake unanenedwa mu Mau ambiri mu makalata onse olembedwa ndi atumwi Paulo, Petro komanso Yohane.

Choyamba, tiyeni timve zomwe Mau akunena pa za ubatizo wa Yesu mu kalata ya Paulo. Kunalembedwa mu Aroma 6:2-7: “Msatero ai. Ife amene tiri akufa ku ucimo, tidzakhala bwanji cikhalire m’menemo? Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwa Kristu Yesu; tinabatizidwa mu imfa yace? Cifukwa cace tinaikidwa m’manda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo kulowa muimfa; kuti monga Kristu anaukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, cotero ifenso tikayende m’moyo watsopano. Pakuti ngati ife tinakhala olumikizidwa ndi Iye m’cifanizidwe ca imfa yace, koteronso tidzakhala m’cifanizidwe ca kuuka kwace; podziwa ici, kuti umunthu wathu wakale unapacikidwa pamodzi ndi Iye, kuti thupilo la ucimo likaonongedwe, kuti ife tisakhalenso akapolo a ucimo; pakuti Iye amene anafa anamasulidwa kuucimo.” 

Mukukhulupilira kuti iye anabatizidwa mwa Yesu, chikhulupiliro cha mtumwi Paulo chinaikidwa mu Uthenga Wabwino kunena kuti Yesu anachita chitetezero cha machimo onse a anthu pamene Iye anabatizidwa. Uthenga Wabwino wa choonadi wachitetezero cha machimo omwe Baibulo likulankhula ndi Uthenga Wabwino wa madzi ndi mwazi, Uthenga Wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pamtanda. Mwa njira ina, Uthenga Wabwino wa chikhululukiro cha machimo onenedwa ndi atumwi mu Baibulo umakamba kuti Yesu anachotsa machimo adziko pobatizidwa.

Tiyeni tsopano timve umboni wa mtumwi Petro pa za ubatizo wa Yesu ndi kunyamula Kwake kwa machimo. Iye anati mu 1 Petro 3:21, “Cimenenso cifaniziro cace cikupulumutsani tsopano, ndico ubztizo, kosati kutaya kwa litsiro lace la thupi, komatu funso lace la cikumbu mtima cokoma kwa Mulungu mwa kuuka kwa Yesu Kristu.” Mtumwi Petro apa akunena kuti ubatizo wa Yesu omwe analandira kwa Yohane Mbatizi ndi chifaniziro cha chipulumutso ndi chitetezero cha machimo. 

Penapake, pamene tikuona pazomwe zinalembedwa mu akalata a mtumwi Yohane zokudza ubatizo wa Yesu, tikuona Baibulo likunena mu 1 Yohane 5:5-8, “Koma ndani iye wolilaka dziko lapansi, koma iye amene akhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu; Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, ndiye Yesu Kristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi. Ndipo Mzimu ndiye wakucita umboni, cifukwa Mzimu ndiye coonadi. Pakuti pali atatu akucita umboni, Mzimu, ndi madzi, ndi mwazi; ndipo iwo atatu ali mmodzi.” Mtumwi Yohane akunenso kuti chipulumutso cha chitetezero cha machimo athu chimakwaniritsidwa pokhulupilira mu Mpulumutsi amene anadza mwa madzi ndi mwazi. Kusiyana Kwa Chikhulupiliro Pakati Pa Atumwi Ndi Atsogoleri Achikristu Chalero


Ndipo tsopano, tingathe kuona apa kuti chikhulupiliro cha atumwi mu Baibulo ndi chosiyana  kwambiri ku chikhulupilira cha azamulungu alero, chomwe chimaikidwa mu mwazi okha wa Yesu. Mukuunikirabe zimenezi pa azamulungu amene amakhulupilira mu mwazi okha wa Yesu, Baibulo limachitira umboni pa zonse ubatizo omwe Yesu analandira kwa Yohane Mbatizi komanso mwazi omwe Iye anakhetsa pamtanda ngati chipulumutso kwa ochimwa. Ndizofunika kwambiri onse a ife lero lino kupeza kumvetsetsa koonadi za ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake ndi kukhulupilira mu Uthenga Wabwinowu wa chitetezero cha machimo bwino bwino. Atumwi anafotokoza momveka bwino mu Baibulo kuti ubatizo wa Yesu (madzi) ndi chifaniziro chomwe chimatipulumutsa ku machimo athu onse (1 Petro 3:21), ndipo ndi mwa Uthenga Wabwino wa chipulumutsowu, Uthenga Wabwino wa ubatizo ndi mwazi wa Yesu, omwe tingathe kugonjetsa dziko mwa kukhulupilira mu chipulumutso choonadi. Ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pamtanda umaonedwa mofanan mu Baibulo onse pamodzi muli Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo. Malembo analemba momveka bwino mu Zipangano zonse kuti Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo ndi odzadza ndi ubatizo ndi mwazi wa Yesu zomwe zinafufuta machimo onse a dziko.

Mateyu, ophunzira wa Yesu ananena mu Mateyu 3:15-16: “Koma Yesu anayankha nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero. Pamenepo anamlola Iye.Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anaturuka m’madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye.” 

Asakanafike pa ndime imeneyi, Mateyu anafotokoza zochitika pansi pamene Yesu anabatizidwa (Mateyu 3:13-14). Ndipo apa mu Mateyu 3:15-16, kwanenedwakuti Yohane Mbatizi anapatsira machimo onse a dziko pa Yesu kudzera mu ubatizo Wake, chipulumutso cha chitetezero cha machimo. Ndipo akuchitira umboni za chipulumutso cha chilungamo cha Mulungu, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, kunena kuti Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi, machimo onse a munthu ali yense mu dziko lino anaikidwa pa Kristu. Motero posenza machimo onse a dziko mwa ubatizo Wake, Yesu kenako anadzichitira umboni Yekha kwa zaka zitatu, kufa pamtanda, kuuka kwa akufa mwa masiku atatu, kukwaniritsa mwathunthu chilungamo kwa okhulupilira ake onse ku machimo onse,  ndipo tsopano akukhala ku dzanja la manja la mpando wa Mulungu Atate. 

 Kuonjezeranso, ophunzira a Yesu analembanso kuti Yesu adzaonekera kachiwiri kwa onse amene alandira chikhululukiro cha machimo mwa kukhulupilira mu ubatizo wa Ambuye komanso mwazi Wake pamtanda, iwo amene akudikilira Ambuye wopanda uchimo. Kunalembedwa mu Ahebri 9:28, “Kotero Kristunso ataperekedwa nsembe kukasenza macimo ambiri, adzaonekera pa nthawi yaciwiri, wopanda ucimo, kwa iwo amene amlindirira, kufikira cipulumutso.” Pamene Yesu anabatizidwa, Mulungu Atate mwini anachitira umboni kwa Yesu, kunena kuti, “Uyu ndiye Mwana Wanga okondedwa,” ndipo Yohane Mbatizi anachitiranso umboni tsiku lotsatira kuti sanali oposa Yesu amene analandira machimo onse adziko kudzera mu ubatizo Wake ndipo anachita chitetezero cha machimowo.

Azipembedzo masiku ano ndi mbuli pa Baibulo komanso osazindikira za ubatizo ndi mwazi wa Yesu omwe unachita chitetezero cha machimo onse a anthu. Ndikukhulupilira kuti ichi ndi chifukwa chakuti maso awo a uzimu ndi otseka, ndipo choncho sangadye pa Mau a kumwamba. Zotsatira zake, Akristu ambiri amaganiza kuti Yesu anasenza machimo adziko mwa Iye yekha mwanjira ina, koma maganizo otere amera kuchokera kuchikhulupiliro chomwe ndi chopanda manyazi chosemphana ndi chipulumutso choonadi, posazindikira kuti Yesu anabatizidwa ndi kukhetsa mwazi Wake kuti apange chitetezero cha machimo onse. Lingaliro limeneli, mwanjira ina, linamera kuchokera ku umbuli chabe wa Akristu a lero omwe sazindikira ubatizo wa Yesu komanso Uthenga Wabwino chitetezero cha machimo.

M’Chipangano Chakale, monga Aroni mkulu wansembe anapereka machimo a Israyeli pamutu pa nyama za nsembe mwa kuika manja pamutu pake, ndipo pamene nyamayi yakhetsa mwazi wake, Aroni ankamasula anthu a Israyeli ku machimo ao. Chimodzi modzinso, ndipo molingana ndi njira yalonjenzoli la chipulumutso, Yesu mwini anadza monga Mwanawankhosa Wansembe wa Chipangano Chatsopano, ndipo motero Yohane Mbatizi anali oyenera ndi okwamira kukhala ngati oimilira wa anthu onse kuti apatsire machimo onse dziko kwa Yesu. Ichi ndi chifukwa chake Atate Mulungu anatuma Yohane Mbatizi myezi isanu ndi umodzi asanatume Yesu. 

Yohane Mbatizi anali kapolo onenedweratu ndi olembedwa mu Buku la Chipangano Chakale la Malaki. Iye anali m’neneri wa Mulungu olembedwa ndi onenedwa mu Malaki 3:1-3, ndipo pamene tibvundukula Mateyu 11:10-11 m’Chipangano Chatsopano, tikuona kuti Ambuye anafunikira kapolo wa Mulungu uyu kuti abatize Iye ndi kupereka machimo onse a anthu pa Iye, kuti Iye apange chitetezero cha machimo onsewa monga Mpulumutsi wa anthu onse. Ndi chifukwa chake Yohane Mbatizi “motero” anapatsira machimo onse a dziko pa Yesu mwa kulemekeza lamulo Lake (Mateyu 3:15). 

Nsembe ya mwanawankhosa ya Chipangano Chakale inalandira ndi kufa chifukwa cha machimo popeza machimo ambiri omwe inasenza pa nthawi imodzi anali a chaka chonse cha a Israyeli, koma mwakuonjezera izi, Yesu Kristu anayenera kulandira tchimo lili lonse la dziko lonse lapansi kudzera mu ubatizo Wake ndi kusiya palibiretu, ndipo Iye anayenera kupachikidwa mpaka kufa kuti apereke mphotho ya machimo onse amenewa ndi kupanga chotetezero chosatha cha machimo a dziko lonse. Ichi ndi chifukwa chake Yesu anayenera kubatizidwa ndi Yohane Mbatizi, kufa pamtanda, kuuka kwa akufa mwa masiku atatu, ndi kupanga chitetezero cha machimo onse, kuti apulumutse kwa muyaya mtundu onse wa anthu ku machimo onse adziko. Ndipo Mulungu wapulumutsa ku machimo ali yense wa kukhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu, muchipulumutso cha Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo.Yohane Mbatizi Anali Nthenga Wa Mulungu


Mau a Mulungu ochitira umboni za Yohane Mbatizi akupezeka mu Mateyu 11:7-15. Tiyeni tonse tiwerenge ndimeyi pamodzi: “Ndipo m’mene iwo analikumuka, Yesu anayambonena ndi makamu a anthu za kwa Yohane, Munaturuka kunka kucipululu kukapenyanji? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi? Koma munaturuka kukaona ciani? Munthu wobvala zofewa kodi? Onani akubvala zofewa alim’nyumba zamafumu. Koma munaturukiranji? Kukaona mneneri kodi? Indetu ndinene kwa inu, wakuposamneneri. Uyu ndiye amene kunalembedwa za iye, kuti, onani Ine nditumiza mthenga wanga pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu m’tsogolo mwanu. Indetu ndinene kwa inu, Sanauke wakubadwa mwa akazi munthu wankuru woposa Yohane Mbatizi; koma iye amene ali wocepa mu Ufumu wa Kumwamba ankulira iye. Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa kumwamba uli wokangamizidwa, ndipo okangamirawo aukwatula ndi mphamvu. Pakuti aneneri onse ndi cilamulo cinanenera kufikira pa Yohane. Ndipo ngati mufuna kulandira, uyu ndiye Eliya amene amati akudza. Amene ali ndi makutu akumva, amve.” Anthu ambiri anaturuka kupita ku chipululu kukaona Yohane Mbatizi, amene ankafuula kwa anthu a Israyeli kuti alape. Yesu mwini anaona zimenezi, ndipo Iye anafunsa gulu lomwe linamzingurila Iye, “kodi n’chifukwa chiani munaturuka kupita ku chipululu? Kodi munapita kukaona munthu obvala zofewa?” Iye kenako ananena kuti iwo amene amabvala zofewa ali m’nyumba za mafumu, pamene Yohane Mbatizi, mtumiki, ankakhala mu chipululu. 

Apa, Yesu ankakamba choonadi kuti Mulungu Atate anasankha Yohane Mbatizi kukhala oimilira wa mtundu wa anthu, ndipo kuti Iye anamtuma iye kwa Yesu kuti adzambatize Iye. Ambuye wathu mwini anachitira umboni za Yohane Mbatizi ndipo anati, “kodi n’chifukwa chiani munaturuka kupita ku chipululu? Kodi munaembekeza kuona chiani kumeneku pamene munapita kwa munthu wa ku chipululu wobvala ubweya wa ngamila? Kodi munapita kukaona munthu obvala zofewa? Anthu otere ali m’nyumba za mafumu. Koma Yohane Mbatizi ndi wamkulu kuposa ngakhale mafumu. Kodi n’chifukwa chiani munaturuka kupita ku chipululu? Kukaona m’neneri? Inde, munapita kukaona m’neneri, koma Yohane Mbatizi anali wamkulu kuposa m’neneri.” Yesu kenako anachitira umboni kuti Yohane Mbatizi anali wamkulu wa obadwa mwa akazi.

Mu nthawi ya Chipangano Chakale, ngakhale mafumu sanali oposa aneneri. Nanga kodi amene anali wamkulu oposa aneneri onse a Chipangano Chakale anali ndani? Anali Yohane Mbatizi. Yesu mwini anachitira umboni kuti Yohane mbatizi anali oimilira wa mtundu onse wa anthu, ananena kuti iye anali wamkulu wa anthu onse. Yesu nayenso ananena kuti Yohane Mbatizi anali mutumiki wa Mulungu amene anatumizidwa pa dziko lino myezi isano ndi umodzi Iye asanabwere, kuti apatsire machimo adziko pa Iye pombatiza Iye, pakuti kunalembedwa: “Koma munaturukiranji? Kukaona mneneri kodi? Indetu ndinene kwa inu, wakuposamneneri. Uyu ndiye amene kunalembedwa za iye, kuti, onani Ine nditumiza mthenga wanga pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu m’tsogolo mwanu” (Mateyu 11:9-10).  Ambuye anachitira umboni poyera kuti m’neneri olonjezedwayo anali osaposa Yohane Mbatizi.

Yohane Mbatizi anachitira umboni za Yesu, kunena kuti “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lace la dziko lapansi!” Anali Yohane Mbatizi amene anachitira umboni kuti Yesu anachotsa machimo onse a dziko, ndipo kuti Iye anali Mwana wa Mulungu; ndipo Yohane anli m’neneri wamkulu wa onse-indedi, wa anthu onse. Popeza Yohane Mbatizi anali wa fuko la Aroni, ndipo iye anagachedwe mobvomerezeka mkulu wansembe womaliza. Pamene mwazindikira ku Chipangano Chakale kuti Mulungu anasankha Aroni kuti akhale mkulu wansembe wa a Israyeli kwa zaka makumi anai, ndipo kuti Iye kwamuyaya anapatsa unsembe umenewu kwa afuko lake, muyenera kukhala odalira kukhulupilira mwa Yohane Mbatizi monga oimilira wa anthu onse komanso wansembe amene anapatsila machimo a dziko kwa Yesu. 

Baibulo likunena kuti, “Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa kumwamba uli wokangamizidwa, ndipo okangamirawo aukwatula ndi mphamvu” (Mateyu 11:12). Ndime imeneyi ikutanthauza kuti Yesu anakhala Mpulumutsi wa ntundu onse wa anthu polandira machimo onse a dziko kudzera mwa Yohane Mbatizi. Yesu mwini anachitira umboni kuti Yohane Mbatizi anapatsira machimo onse pa Iye. Mu Mateyu 11:12, Yesu analankhula za Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo onse a mtundu wa anthu, kunena kuti machimo onse anaikidwa pa Iye kudzera mu ubatizo opatsidwa ndi Yohane mbatizi. Ambuye analankhula za Uthenga Wabwino wa ubatizo Wake ndi mwazi, ndipo iwo amene a khulupilira mu Uthenga Wabwino wa kumwamba anakhulupilira kuti Yesu anapachikidwa mpaka kufa chifukwa Iye anasenza machimo onse a dziko kudzera mu ubatizo Wake. Umboni Wa Zakariya


Tsopano, tiyeni tichite chidwi ndi atate a Yohane mbatizi Zakariya ndi kumvetsera umboni anapereka pamene anamva kwa mngelo za kubadwa ndi tsogolo la utumiki wa mwana wake. Kunalembedwa mu Luka 1:67-88: “Ndipo atate wace Zakariya anadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nanenera za Mulungu, nati,Wolemekezeka Ambuye, Mulungu wa Israyeli; Cifukwa Iye anayang’ana, nacitira anthu ace ciombolo, ndipo Iye anatikwezera ife nyanga ya cipulumutso, mwa pfuko la Davide mwana wace, (Monga Iye analankhula ndi m’kamwa mwa aneneri ace oyera mtima, a kale lomwe), Cipulumutso ca adani athu, ndi pa dzanja la anthu onse amene atida ife; Kucitira atate athu cifundo, Ndi kukumbukira pangano lace lopatulika; Cilumbiro cimene Iye anacilumbira kwa Abrahamu atate wathu, kutipatsa ife kuti titalanditsidwa ku dzanja la adani athu, Tidzamtumikira Iye, opanda mantha, M’ciyero ndi cilungamo pamaso pace, masiku athu onse. Eya ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa mneneri wa Wamkulukulu: Pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zace: Kuwapatsa anthu ace adziwitse cipulumutso Ndi makhululukidwe a macimo ao, Cifukwa ca mtima wacifundo wa Mulungu wathu. M’menemo mbanda kuca wa kumwamba udzaticezera ife; Kuwalitsira iwo okhala mumdima ndi mthunzi wa imfa; kulunjikitsa mapazi athu mu njira ya mtendere. Ndipo mwanayo akula nalimbika mu mzimu wace, ndipo iye anali m’mapululu, kufikira masiku kudzionetsa yekha kwa Israyeli.” 

Apa, Zakariya anali kulosera za mwana wake Yohane Mbatizi monga mtumiki wa Mulungu, kufotokoza kuti adzakhala mtumiki otani komanso adzakwaniritsa bwanji unsembe wake. Zomwe Zakariya ankanena apa, kuti Yohane Mbatizi “Kuwapatsa anthu ace adziwitse cipulumutso Ndi makhululukidwe a macimo ao,” iye ananenera za Uthenga Wabwino wa Mau a chipulumutso. Yohane Mbatizi anali mboni ya Yesu kwa onse a ife amene takhulupilira mwa Yesu. Ndipo iye anachitiranso umboni za Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo kwa ife, kunena kuti tapulumutsidwa pokhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Yohane anaphunzitsa ife chidziwitso kuti talandira chikhululukiro cha machimo pokhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo athu onse. 

Luka 1:76 ikuti, “Eya ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa mneneri wa Wamkulukulu: Pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zace.” Ndimeyi ikutanthauza kwa Yohane mbatizi. Kuchita chitetezero cha machimo athu, Yesu anasenza machimo onse a dziko mwa ubatizo Wake. Ndipo Yohane mbatizi, mukunena kuti iye anapereka machimo onse a dziko kwa Yesu kudzera mu ubatizo omwe anampatsa iye, kwapanga chipulumutso cha chitetezero cha machimo kudziwika kwa ife.

Ife tonse okhulupilira tingazindikire choonadi apa kuti Yesu anatenga machimo a dziko ndi kupita nao pamtanda kudzera mu ubatizo omwe iye analandira kwa Yohane Mbatizi ndi kupanga kuthekera kuti onse amene akhulupilira mu chitetezero cha machimo cha ngwirochi apulumutsidwe. Zikomo ku Mau a Mulungu okamba kuti Yesu watipulumutsa ife mwa ngwiro, tiri ndi kuthekera kokhulupilira mwa Ambuye wathu, ndipo pokhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu, tingapulumutsidwe. Ndipo kudzera mwa Yohane Mbatizi, ali yense wazindikira kuti Yesu ndi Mpulumutsi amene anapanga chitetezero cha machimo onse a dziko.

Pokha pokha ngati tadziwa ubatizo wa Yohane Mbatizi anapatsa kwa Yesu, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, kodi ena a ife tikanakhulupilira bwanji mwa Yesu ngati Mpulumutsi wathu ndi chitsimikizo chodzadza? Popanda kudziwa Uthenga Wabwino wa choonadi wa chitetezero cha machimo, palibe chipulumutso kapena moyo wosatha. Ngati inu mwakhulupilira mwa Yesu popanda kudziwa utumiki wa Yohane Mbatizi, ndiye kuti chikhulupiliro chanu si cha ngwiro ndipo inu mukukhala moyo operewera wa chi Kristu. Ndipo mukudalira pa ziphunzitso zaumulungu zokha. Koma, ngati mukudziwa choonadi ndi kuzindikira kuti Yohane Mbatizi anali ndani, ndipo ndi ubatizo otani omwe iye anapatsa Yesu pa chipulumutso cha anthu ndi chikhululukiro cha machimo, kenako mudzapulumutsidwa ku machimo anu onse mwa chikhulupiliro. 

Munthu asanachimwe, kunalibe tchimo, ndipo choncho panalibe chifukwa chofunira chikhululukiro cha machimo. Koma pamene Adamu ndi Hava anachimwa, tchimo linalowa mu dziko, ndipo chitetezero chinayenera kuchitika ku tchimo lili lonse. Mu nthawi, popita m’masiku a Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, ndi kufikira Eksodo wa mbeu ya Yakobo kuchokera ku a Aigupto, pamene anthu a Israyeli anaoloka Nyanja yofiira ndi kukhala m’chipululu, Mulungu anapatsa lamulo kwa iwo kudzera mwa Mose. Mu nthawi yomweyo, Mulungu anapatsanso ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe ku kachisi, yomwe kudzera mwa iyo ankapanga chitetezero cha machimo ao popatsira machimo ao ku nyama za nsembe monga mbuzi, ng’ombe zamphongo kapena ana a nkhosa. Kuchokera pamenepo nthawi ya lamulo inayamba, ndipo nthawi iyi inali nthawi ya zowawa chifukwa lamulo silikanabweretsa chikhululukiro cha machimo chamuyaya komanso chokwanira, choncho a Israyeli anayenera kuyembekeza Mesiya ali mkudza.

Nthawi ya lamuloli inatha m’maso mwa Mulungu ndi ubatizo wa Yesu omwe ndi chizindikiro cha chiyambi cha nthawi ya chisomo. Nsembe zonse za Chipangano Chakale zomwe zinali chithunzithunzi cha chipulumutso cholonjezedwa cha Chapangano Chakale zinatha ndi ubatizo wa Yesu omwe analandira kwa Yohane Mbatizi. Mwanjira ina chipulumutso ku machimo cholonjezedwa chinakwaniritsidwa kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, chomwe chinapanga chitetezero cha tchimo lili lonse la mtundu wa anthu onse.

Zakariya, wansembe ochokera kunyumba ya mkulu wansembe, anamva kuchokera kwa Mulungu kuti Iye adzampatsa iye mwana wa mwamuna. Mukuona kwa munthu kunali kosatheka kwa mzimayi wamkulu kubala mwana, koma mkazi wa Zakariya anatengadi pakati, ndiponso namwali Maria anatenga pakati. Mngelo anaonekeranso kwa Maria ndi kunena kwa iye, “Pakuti wapeza chisomo ndi Mulungu,” ndipo Maria anati, “Onani, mdzakazi wa Ambuye; kukhale kwa ine monga mwa Mau anu” (Luka 1:38). Maria anapeza chisomo cha Mulungu ndipo anadalitsidwa kubala Mwana Yesu Kristu.

Dalitso limeneli, koma, silinkaoneka ngati dalitso mkomwe nthawi imeneyo, monga mwa lamulo la chi Yuda ankapatsa chilango chowawa ngati mzimayi osakwatira wapezeka ndi pathupi. Ndipo tsopano, kukhala ndi mwana kunja kwa ukwati kunkabweretsa mabvuto aakulu amanyazi ndi kuononga moyo wa mzimayi, koma mwachisomo cha Mulungu, Maria anadalitsidwa ndi ulemelero wa pamwamba komanso waukulu kuposa mabvuto a thupi lake. Mwanjira ina, pamene anabvomereza chikhulupiliro chake, Maria anakhala ndi pakati. Kutenga pakati kwake kwa Yesu zinanenedwanso kale ndi mngelo wa Mulungu. Monga chonchi, Yesu Kristu Ambuye wathu anabadwa kudzera mwa thupi la namwali Maria.

Maria sanali wa fuko la Aroni. Anali wafuko la Yuda. Mwamuna wake Yosefe analinso wa fuko la Yuda. Ichi ndi chifukwa chake monga mfumu ya mafumu, Yesu Kristu anadza ngati wafuko la chifumu. Ndipo Yohane Mbatizi anadza kudzera mu mbadwo wa Aroni, kuchokera kunyumba ya wamkulu wansembe. 

Asanatume Yesu, Mulungu Atate anatuma Yohane Mbatizi, mtumiki Wake komanso m’neneri. Pokhapo akananenera za Chipangano Chakale kuti chikwaniritsidwe pofuna kuti ife tikhulupilire mwa Mulungu. Ndipo chifukwa ofesi ya mkulu wansembe linakhazikitsidwa ndi Mulungu kwa muyaya, monga mbeu ya Aroni, Yohane Mbatizi anali mkulu wansembe omaliza wa anthu onse amene akanapatsira machimo a dziko kwa Yesu kudzera mu ubatizo omwe anampatsa Yesu.

Aroni anali mkulu wansembe oyamba wa a Israyeli, ndipo iye anali mkulu wa mbale wake Mose. Agogo ake a Aroni aakulu anali Levi (m’modzi mwa ana khumi ndi awiri a Yakobo), agogo ake anali Kohati, bambo ake anali Amramu, ndipo amayi ake anali Yochebedi, komanso mlongo wake wa mkulu Miriamu (Eksodo 6:16-20). Aroni anali ndi ana amuna anai otchedwa Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara (Eksodo 6:23; Numeri 3:2). Kuchokera pa nthawi imene Mose anaitanidwa ndi Mulungu kuti atsogolere anthu ake kuchoka ku Aigupto, Aroni ankamuthandiza iye ndipo ankalankhula m’malo mwake poti Mose anali wa chibwibwi (Eksodo 4:10, 7:10). Ndipo pamene pangano pakati pa Mulungu ndi anthu a Israyeli linatsimikizika paphiri la Sinai, Aroni anatenga mbali muzochitika komanso Mulungu pamodzi ndi Mose komanso akulu akulu makumi asano ndi awiri a Israyeli, zomwe zikuonetsa kuti iwo anali oimilira a anthu a Israyeli (Eksodo 24:1-11). Ndipo pamene kachisi inamangidwa kudzera mwa Mose chifukwa cha anthu a Israyeli, Aroni ndi ana ake amuna anai anadzodzedwa ndi Mulungu ndi kuayeretsa monga ansembe ake (Eksodo 28:21, 40:13-16). 

Aroni anatumikira monga mkulu wansembe oyamba wa a Israyeli kwa zaka makumi anayi, ndipo pa chifukwa ichi mtundu wa Rubeni anadandaula za kupalidwa kwake ku udindo wa unsembe. Choncho kuonetsa kuti nyumba ya Aroni inali yosankhidwa, Mulungu analamula mtundu uli onse, wa a Israyeli kuti abweretse ndodo, ndipo ndodo ya Aroni inapatikizidwa m’maere kuimilira mtundu wa Levi. Mwa ndodo khumi ndi ziwirizi inali ndodo ya Aroni yomwe inachita maluwa, kuonetsa poyera kuti unsembe wa nyumba yake unapatsidwa ndi Mulungu kuti atumikire anthu a ku Israyeli (Numeri 17:1-10). 

Pamene Aroni anamwalira kwa zaka 123, zobvala zake za unsembe zinabvekedwa pa Eliazara mwana wake, Eliazara anakhala mkulu wansembe m’malo mwa Aroni (Numeri 20:23-29). Olemba Buku la Ahebri kuchitira umboni kuti Aroni anali mkulu wansembe wa padziko, pamene Yesu anali Mkulu Wansembe wa ufumu wa kumwamba (Ahebri 7:11-28).Palibe Chokaikitsa Kuti Yohane Mbatizi Anali Mkulu Wansembe Amene Anabatiza Yesu Mwa kuika Manja Kuti Atetezere Machimo a Dziko Lapansi


Yesu mwini anachitira umboni kuti Yohane Mbatizi anali oimilira wa mtundu onse wa anthu, monga Iye ananenera mu Mateyu 11:10-11: “Uyu ndiye amene kunalembedwa za iye, kuti, onani Ine nditumiza mthenga wanga pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu m’tsogolo mwanu. Indetu ndinene kwa inu, Sanauke wakubadwa mwa akazi munthu wankuru woposa Yohane Mbatizi; koma iye amene ali wocepa mu Ufumu wa Kumwamba ankulira iye.”  Monga Yesu anachitira umboni apa, Yohane Mbatizi anakwaniritsa unsembe wake opatsira machimo a anthu kwa Yesu.Kulowa Kumwamba Kunayambira Masiku a Yohane Mbatizi


Baibulo likunena mu Marko 1:1-8: “CIYAMBI cace ca Uthenga wabwino wa Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu. Monga mwalembedwa m’Yesaya mneneri, Ona, ndituma mthenga wanga patsogolo pa nkhope yanu, Amene adzakonza njira yanu; Mau wopfuula m’cipululu, Konzani khwalala la Ambuye, Lungamitsani njira zake; Yohane anadza nabatiza m’cipululu, nalalikira ubatizo wakutembenuka mtima wakuloza ku cikhululukiro ca macimo. Ndipo anaturuka a ku dziko lonse la Yudeya, ndi a ku Yerusalemu onse; nadza kwa iye nabatizidwa ndi iye mumtsinje Yordano, poulula machimo ao. Ndipo Yohane anabvala ubweya wa ngamila, ndi lamba la cikopa m’cuuno mwace, nadya dzombe ndi uchi wa kuthengo. Ndipo analalikira, kuti, Wondipambana ine mphamvu akudza pambuyo panga, sindiyenera kuwerama kumasula lamba la nsapato zace ine. Ndakubatizani ndi madzi; koma Iye adzakubatizani ndi Mzimu Woyera.”

 Nthawi zonse pamene tikuchita chinthu chofunika, timakonzekera choyamba. Momwemonso, Mulungu anakonza Yohane Mbatizi ngati phazi loyamba kuti achotse machimo a dziko lapansi. 

 Tiyeni tione Yohane Mbatizi bwinobwino apa, amene anakonza njira ya ufumu wa kumwamba. Pamene tibvundukura Buku la Malaki m’Chipangano Chakale, tingathe kuona kuti ansembe pa nthawi imeneyo anaonongeka. Choncho chifukwa cha izi, kunalibe wansembe owongoka mpaka pamene Yesu anabwera pa dziko lino kwa nthawi yoyamba monga Ambuye wathu. Ansembe a nthawiyo analinso owonongeka chifukwa iwo anataya malamulo a Mau a Mulungu ndi kunyalanyaza ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe kokhazikitsidwa ndi Mulungu ndi malamulo Ake. Choncho Mulungu anayenera kubweretsa pa dziko lino wansembe amene adzakhala mthenga Wake komanso nkhoswe. Ichi ndi chifukwa Chake Mulungu anatuma mthenga Wake, ndipo mthengayo ndi osaposa Yohane Mbatizi amene anakonza njira ya ufumu wa kumwamba.

 Yohane Mbatizi anatumizidwa pa dziko lino asanatume Yesu. Kupatsira machimo a Israyeli pamutu pa mbuzi ya moyo, Mulungu nthawi zonse ankagwiritsa ntchito mkulu wansembe ngati oimilira wao, ndipo pachifukwa ichi, anayenera kutumiza Yohane Mbatizi. Ichi ndi chifukwa Chake Mulungu anasankha Yohane Mbatizi kwa mtundu wa anthu. Komabe, chifukwa Yohane Mbatizi ankakhala yekha mu chipululu ndi kufuula kwa anthu a Israyeli kuti atembenuke.

 Marko 1:2-3 anatenga malembedwe a Yesaya m’neneri ndi kunena kuti, “Monga mwalembedwa m’Yesaya mneneri, Ona, ndituma mthenga wanga patsogolo pa nkhope yanu, Amene adzakonza njira yanu; Mau wopfuula m’cipululu, Konzani khwalala la Ambuye, Lungamitsani njira zake.” Kodi munthu ameneyu ankafuula chiani ku chipululu? Iye ankafuula za ubatizo wakulapa kuti alandire chikhululukiro cha machimo.

Mu Baibulo, Mau onena kuti ubatizo ndi (baptisma) mu chi Greek, omwe akutanthauzanso kunyika kapena kukwirira, akutsindika tanthauzo la kuika manja m’Chipangano Chakale. Kunena kwina, akutanthauza kupatsira kapena kusamutsa china chake.

Ubatizo omwe Yohane Mbatizi ankafuula unali pawiri. Ubatizo oyamba unali ubatizo wakulapa, omwe unkaitana ali yense kubwerera kwa Kristu Mesiya, Mwanawankhosa Wa nsembe yosatha wa kumwamba (Ahebri 10:12), ndipo ubatizo wa chiwiri unali umene Yohane Mbatizi anapatsa Yesu, umene machimo onse anapatsidwa kwa muyaya pa thupi la Yesu. Monga m’neneri, Yohane Mbatizi choncho ankafuula kwa ali yense kuti atembenuke ku uchimo ndi kukhulupilira mwa Yesu, amene anachotsa machimo a dziko kudzera mu ubatizo Wake, komanso anali kuloza kuti ali yense anali ochimwa pamaso pa Mulungu. Anthu ambiri ndiyeno anadza kwa Yohane Mbatizi ndi kulandira madzi a ubatizo kutsimikiza kuti iwo wokha anali ochimwa pamaso pa Mulungu. 

Ubatizo ukutanthauza kutsuka, kupatsira, komanso imfa. Yohane Mbatizi anabatiza anthu a Israyeli kubvomereza kuti iwo anali ochimwa pamaso pa Mulungu ndi kutembenukira kwa Iye. Ndipo ubatizo wina omwe iye anapatsa Yesu, unali ubatizo wa chipulumutso kwa anthu onse, omwe unapatsira machimo onse kwa Mwana wa Mulungu ku chikhululukiro cha machimo. Yesu anati mu Mateyu 3:15, “Balola tsopano: Pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero.” Mau a chitetezero cha machimo onenera za kanyamlidwe ka machimo ka Yesu anakwaniritsidwa kwa thunthu. 

Mu Kristu ali yense okhala pa dziko lino ayenera kukhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo. Kwa ife, Yohane Mbatizi anapereka kwamuyaya machimo onse adziko kwa Yesu pobatiza Iye kuti apange chitetezero cha machimo monga Ambuye anamlamulira iye, ndipo umu ndi m’mene Yohane Mbatizi anakonzera ufumu wa kumwamba kuti ife tikalowe pokhulupilira mwa Yesu, ndipo umu ndi m’mene Yesu anakhalira njira ya kumwamba. 

Kunalembedwa mu Marko 1:14-15: “Ndipo ataperekedwa Yohane, Yesu anadza ku Galileya, nalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, nanena, nthawi yakwanira, ndipo ufumu wa Mulungu wayandikira; tembunukani mtima, khulupilirani Uthenga Wabwino.” Uthenga Wabwino ukutanthauza nkhani yabwino, ndipo ndi “euaggelion” mu chi Greek. Ukutanthauza Uthenga Wabwino wa kumwamba onena kuti pamene Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi ku chitetezero cha machimo, Iye analandira machimo onse adziko ndi kuchotsapo onse. Chifukwa cha ubatizowu, machimo onse adziko anabwera pa Yesu kudzera mwa Yohane Mbatizi pamene Yesu anabatizidwa. Mwanjira ina, Uthenga Wabwino omwe wabweretsa chitetezero cha machimo a anthu ndi osaposa Uthenga Wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pamtanda. Machimo onse a dziko akutanthauza machimo a munthu ali yense, ndipo machimo amenewa sakuphatikiza machimo anu okha, koma machimonso a dzidzukulu zanu. Kuonjezerapo, machimo anu akutanthauza onse akale, atsopano ndi machimo amtsogolo, kuphatikiza osati machimo okha amene m’machita m’machitidwe anu koma machimonso amene m’machita m’maganizo anu. Ndipo dziko apa likutanthauza dziko lonse lapansi kuchokera pachiyambi pake kufikira kumapeto ake, ndipo Yesu wapanga chitetezero cha machimo onsewa ochitidwa mu dziko lapansi.Yohane Mbatizi Anadza Mwanjira Ya Chilungamo


Yohane Mbatizi anadza mwa njira ya chitetezero cha machimo ndi njira ya chilungamo, kupereka chipulumutso choonadi kwa anthu, monga kunalembedwa mu Mateyu 21:32, “Popeza Yohane anadza kwa inu m’njira ya cilungamo.” Yohane Mbatizi anatumizidwa pa dziko lino ndi Mulungu kuti adzaike machimo onse a munthu ali yense mu dziko lino pa Yesu, ndi kutsogolera onse ku njira yopapatiza, njira yachilungamo, kuti alandire chikhululukiro cha machimo mwa chikhulupiliro. Ndipo pamene Yohane Mbatizi anapatsira machimo onse adziko pa Yesu ndi kuchitira umboni mwa njira imeneyi ya chitetezero cha machimo, zikomo chifukwa cha umboni wake, anthu ambiri anapulumutsidwa pozindikira ndi kukhulupilira mu chipulumutso choonadi ichi.

Yesu anati mu Mateyu 21:32, “Popeza Yohane anadza kwa inu m’njira ya cilungamo, ndipo simunamumvera iye; koma amisonkho ndi akazi aciwerewere anammvera iye; ndipo inu, m’mene munaciona, simunalapa pambuyo pace, kuti mumvere iye.” Pamene Yesu ananena apa kuti, “Yohane anadza kwa inu mnjira yachilungamo,” iye ankakamba zoonadi kuti Yohane Mbatizi anali mkulu wansembe otsiliza wa Chipangano Chakale (Mateyu 11:13), ndipo kuti iye anapatsira machimo onse a anthu pobatiza Iye. 

Kodi nanga, n’chifukwa chiani, amisonkho ndi akazi achiwerewere anakhulupilira mu ubatizo wa Yesu monga chipulumutso chao, omwe Yohane Mbatizi anapatsira machimo onse adziko kwa Ambuye? Tiyenera kuganiza apa mosamala chifukwa chiani kuti akazi achiwerewere ndi amisonkho anapulumutsidwa ku machimo ao pokhulupilira mu ntchito ya chilungamo yomwe Yesu ndi Yohane Mbatizi anachita, pamene ena ambiri anaongedwa posakhulupilira kuti Yohane Mbatizi anapatsira machimo onse adziko pa Yesu. Amisonkho komanso akazi achiwerewere anali ochimwa ofanana odzadza ndi machimo. Ngati Yohane Mbatizi sakanabatiza Yesu kuti apatsire machimo onse adziko pa Iye kamodzi kokha, amisonkho ndi akazi achiwerewere sakanapulumutsidwa ku machimo ao onse omwe anali andiweyani monga mtambo. Koma iwo anakhulupilira muchipulumutso cha Yesu ndi mitima yao yonse, ndipo iwo anapulumutsidwa mwa chikhulupiliro chimenechi-chomwe ndi, kukhulupilira kuti Yohane Mbatizi anapatsira machimo onse adziko pa Yesu kudzera mu ubatizo kuti Iye achite chitetezero cha machimo onse kamodzi kokha kwatha. Ndipo chifukwa iwo anakhulupilira mwa Yesu monga Mwana wa Mulungu komanso Mwanawankhosa Wansembe amene anatumizidwa ndi Atate kupulumutsa iwo ku machimo ao onse, iwo anakhululukidwa ku machimo onse adziko ndi kupeza chipulumutso chao chosatha mwa chikhupiliro.

Popanda ntchito yomwe Yohane Mbatizi anachita mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, kodi ife tikanalandira bwanji chipulumutso mwa chukhulipiliro? Mwina munganene kuti ziribe ntchito chifukwa m’makhulupilira mwa Yesu mwanjira ili yonse. Koma kupulumutsa inu ku machimo anu onse, Mulungu anakwaniritsa chipulumutso cha chikhululukiro cha machimo popereka machimo anu onse kwa Yesu mwa ubatizo omwe Yohane Mbatizi anabatiza Yesu. Nanga kodi Yesu angakhale Mpulumutsi wanu ngati simukhulupilira mu chitetezero ichi cha machimo chomwe Iye anapanga? Kodi mungabadwe mwatsopano pokhulupilira mwa Yesu m’njira ili yonse yomwe mwasankha, ngakhale kuti mwakwirira machimo anu popanda kuika onse pa Ambuye mwa ubatizo? Ganizani za izi. 

Pofuna kupulumutsa inu ku machimo komanso ku mphotho zawo, Mulungu anatuma Yohane Mbatizi kudziko lino, ndipo Iye anankoza kuti aike machimo anu pa Yesu kudzera mwa Yohane Mbatizi. Mu kuunika kwa choonadi chakuti Mulungu anaganiza ku patsira machimo anu onse kwa Yesu kudzera mu ubatizo, simungapulumutsidwe ngati inu munyalanyaza lingaliro la Mulungu. Ngati mukana ganizo la Mulungu kuti akupulumutseni kudzera mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu, kutali ndi chipulumutso cha Mulungu, mudzapita ku gahena pokana chikonzero chake. Choncho ndikupemphani inu kuti muganize mosamala komanso moona, ndi kuunikira pa mau a Mulungu a choonadi kuti tione chinthu choyenera kuchita.

Chinthu choyenera kuchita ndi choti inu mupulumutsidwe ku machimo pokhulupilira mwa Yesu malingana ndi chisankho cha Mulungu. Kodi muli ndi zotani m’maganizo anu tsopano? Kodi mudakali kukumbatira maganizo anu oipa? Muyenera kutaya maganizo anu onse ndi kukhulupilira mu choonadi choti Yesu anakhululukira machimo anu onse kudzera mu ubatizo Wake wa chitetezero cha machimo omwe analandira kuchokera kwa Yohane Mbatizi. Khulupilirani mu chifunirochi cha Mulungu, amene wakupulumutsani kudzera mwa madzi ndi Mzimu. Ngati mwakhulupilira kuti machimo anu onse anapatsidwa kwa Yesu, ndiye mudzakhala opanda uchimo chifukwa cha chikhulupilirochi, mudzakhala munthu olungama kenako, ndipo anthu onse olungama amene akhulupilira mu choonadichi adzapita kumwamba malingana ndi lamulo la chisomo la Mulungu.

Koma ngati mukana Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo ndi kunyalanyaza  kubvomereza kuti machimo anu onse anaperekedwa pa Yesu ndiye kuti mukukana chipulumutso cha Mulungu. Kodi mungapitilizebe kukana njira yoona imene Yohane Mbatizi anampangira Yesu? Muyenera kuzindikira apa kuti ngati mukana choonadi, ndiye kuti mukukana chifuniro chonse cha Mulungu ndi chikonzero chonse, ndipo mudzadzitembenuza nokha ku ochimwa onyansa kukana choonadi ndi maganizo anu.

Patatha tsiku La ubatizo Wa Yesu, pafupi ndi malo amene Yohane  Mbatizi anambatizira Yesu, anachitira umboni Ambuye nafuula, “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” pakubvomera motero machimo onse a dziko, Yesu anapachikidwa ndi kufa patatha zaka zitatu kupereka mphotho ya machimo amenewa.

Tchimo ndi losalemera. Lilibe mtundu uliwonse, fungo lililonse, maonekedwe aliwonse, kapena kusokosa. Ndipo chifukwa inu simungapeze ndi nzeru za kuthupi mwa kuona, kununkhiza, kulawa, kapena kumva, mwa inu nokha simungamvere. Osayesera kumvera mwa maganizo anu okha kuti machimo onse adziko komanso machimo anu anasowa. Kumvera kumasintha. Koma Mau a Mulungu, choonadi chomwe chinafufuta machimo athu onse adziko, ndi chosasintha kwa muyaya. Choncho ndipempha inu kuti mumve Mau a choonadi a Mulungu mwa chikhulupiliro, pokhulupilira muzomwe Yohane Mbatizi anachitira umboni: “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” Yesu anachitira umboni pa chipulimutso kwa zaka zitatu, kulalikira, “Ine ndine njira, coonadi ndi moyo.” Mulungu mwini akuchitira umboni kuti chitetezero cha anthu kumachimo chinachitika mwa ubatizo Wake ndi mwazi, ndipo Iye akutiuza ife kuti tikhale monga ophunzira ake ndi kulalikira Uthenga Wabwino wa ubatizo Wake ndi mwazi. 

M’neneri Yesaya akuti: “Munene inu zontonthoza mtima kwa Yerusalemu, nimupfuulire kwa iye, kuti nkhondo yace yatha, kuti kuipa kwace kwakhululukidwa; kuti iye walandira mowirikiza m’dzanja la Yehova, cifukwa ca macimo ace onse” (Yesaya 40:2).

Indedi, kupanga chitetezero cha machimo anu ndi anga, Yesu analandira machimo onse kudzera mu ubatizo omwe Iye analandira kwa Yohane Mbatizi, Iye anafa pamtanda kulipila mphotho ya machimo onsewo, ndipo Iye anagonjetsa imfa mwa kuuka kwa akufa. Chinthu choyamba chimene Mulungu anachita kuti achotse machimo athu onse ndi kupulumutsa ife chinali kutumiza Yohane Mbatizi pa dziko lino. Mwanjira ina, kunali kupulumutsa ife ochimwa ku machimo athu onse kuti Mulungu anatuma mtumwi wa chifumu. Baibulo limanena izi momveka bwino, poti kunalembedwa mu Malaki 3:1: “taonani ndituma nthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso Panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza kukachisi wace modzidzimutsa; ndiye nthenga wa cipangano amene mukondera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.” Yohane Mbatizi ndi nthenga wa Mulungu olonjezedwa kutumizidwa apa.

Mtumiki wa Mulungu uyu, Yohane Mbatizi, anaika machimo onse pa Yesu kudzera mu ubatizo Wake. Iyi ndi njira yomwe Yohane Mbatizi anakonzera ufumu wa kumwamba kwa Yesu kubweretsa chikhululukiro cha machimo; iyi inali njira ya chipulumutso chathu; ndipo kulibenso njira ina koma iyi. Yesu anati, “Ine ndine njira, coonadi ndi moyo.” Njira ya chipulumutso inali yoti Yesu apange chitetezero cha machimo onse adziko kudzera mu manja a ubatizo a Yohane Mbatizi. Ichi ndi choonadi, ndipo pokhulupilira mu Uthenga Wabwino wa choonadiwu talandira moyo wa tsopano.

Nanga inu bwanji? Kodi munapatsira machimo anu onse ndi machimo a dziko kuli Yesu pamene Yohane anambatiza Iye? Kodi mukukhulupilira mu zimenezi? Ichi chinali chikonzero  chokonzedweratu cha Mulungu cha chipulumutso ndi mapangidwe odabwitsa oyenera nzeru Zake. Koma ngati mukana ichi, simuzaloledwa kubwera mkhola la Mulungu pokana njira yace ya chilungamo ya chipulumutso. Choncho ndi kupemphani inu kukhulupilira m’njira ya chipulumutso, mu choonadi kuti Mulungu anapatsira machimo anu onse kuli Yesu kudzera kwa Yohane Mbatizi. Ndikudandaulirani inu nonse kuti musakane njira ya moyo. 

Yesu ananena mu Mateyu 11:12, “Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa kumwamba uli wokangamizidwa, ndipo okangamirawo aukwatula ndi mphamvu.” Kunena kuti okangamira atenga ufumu wa kumwamba ndi mphamvu zikutanthauza kuti olowa kumwamba ndi iwo amene akhulupilira kuti machimo onse a dziko anasamutsidwa kwa Yesu pamene Iye anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi, chifukwa anthu amenewo alibe tchimo. Ufumu wa Mulungu, kumwamba, uli wa iwo amene anakhulupilira kuti machimo ao onse anapasidwa kuli Yesu kudzera kwa Yohane Mbatizi, ndipo chipulumutso chanafika kwa ali yense wakhulupilira mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo onena kuti Yohane Mbatizi anapatsira machimo onse pa Yesu. 

Okondedwa anzanga okhulupilira, ndindani adachita kuthekera kuti ife tikhulupilire mwa Yesu ndi kupanaga njira ya kumwamba kwa ife? Ndi Yohane Mbatizi. Monga m’mene Mulungu analonjezera kutumiza nthenga Wake kuti akonze njira ya Ambuye, Yohane Mbatizi anapatsa machimo athu onse kwa Yesu Kristu, ndipo mwakuchita choncho, Iye adapanga kuthekera kwa ife kuti tikhale opanda tchimo ndi oyera ndi ololedwa ngati ana Mulungu, ndipo Iye anakonzera ife kuti tikalowe ufumu wa kumwamba. Wanthenga ameneyu, Yohane Mbatizi, otumizidwa ndi Mulungu mwini anakonza njira ya kumwamba ngati oimilira wathu kuti ife tikalowe ufumu wa kumwamba. Iye anakonza njira kwa ife kuti tibadwenso mwatsopano.

Kunalembedwa mu Mateyu 3:13-17: “Pamenepo Yesu anacokera ku Galileya nadza ku Yordano kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye. Koma Yohane anati amkanize, nanena, Ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi? Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse ca Mulungu motero. Pamenepo anamlola Iye. Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anaturuka m’madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye; ndipo onani, mau akucokera kumiyamba, akuti Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.” 

Yohane Mbatizi anachita chinthu cholondola popereka machimo onse a munthu ali yense mu dziko lino kwa Yesu, ndipo uwu ndi Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, chilungamo cha Mulungu, komanso njira ya chipulumutso younikiridwa kudzera mwa Yohane Mbatizi. Chipulumutso chimakwanitsidwa pokhapo ngati tazindikira Uthenga Wabwino umenewu wa chitetezero cha machimo m’myoyo yathu ndi kukhulupilira ndi mtima onse mu ubatizo, mwazi ndi kuuka kwa Yesu zomwe zikupanga Uthenga Wabwino umenewu. Kudzera mu ubatizo Wake, Yesu anakwaniritsa chilungamo chonse cha Mulungu. Pamene Iye analandira machimo athu onse omwe anapatsidwa ndi Yohane Mbatizi, tchimo lili lonse linaikidwa pamutu Pake. Ndipo pamene Iye anachita chitetezero cha machimo a munthu ali yense ndi imfa Yake pamtanda, Iye anamaliza chipulumutso cha anthu onse.

Buku la Ahebri likunena kuti Yesu ndi Mkulu Wansembe wa kumwamba malingana ndi dongosolo la Melikizedeke. Yesu Kristu analibe mbadwo kapena wa fuko la Aroni. Iye analibe mbadwo chifukwa Iye sanali mbeu ya munthu ali yense koma anali Mwana wa Mulungu, Mlengi amene anapanga ife komanso amene anadzipeza Yekha. Koma kupatula izi, Iye anasiya ulemelero wa kumwamba ndi kudza pa dziko lino kudza pulumutsa anthu Ake. Kunena motsindika, pamene anthu Ake odalitsika anagwa m’mayesero a Satana ndipo anabvutika pansi pa dzingwe za mdierekezi, Yesu anabatizidwa mu mtsinje wa Yordano kuti atetezere machimo ao.

Tiyeni tonse tiwerenge Mateyu 3:15 kachiwiri ndi mau amodzi: “Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse ca Mulungu motero. Pamenepo anamlola Iye.” Apa, tikuona Yesu akulamula oimilira wa dziko kuti ambatize Iye. Pamene Yohane Mbatizi walemekeza lamuloli Yesu anaweramitsa mutu Wake ndipo anabatizidwa ndi iye. Monga ngati mkulu wansembe wa Chipangano Chakale anaika manja ake pa mbuzi ya moyo kupatsira machimo onse a chaka a anthu a Israyeli, momwemonso ndi m’mene anachitira Yohane kuika manja ake pamutu pa Yesu ndi kupatsira machimo onse a dziko pa Iye pombatiza Iye kuti abweretse chikhululukiro cha machimo onse kwa anthu.Mulungu Wapulumutsa Ife Molingana Ndi Dongosolo La Oimilira


Pamene purezindeti wa dziko lanu wapanga ulendo kuyenda ku dziko lina ndi kupereka zolankhula nyumba yake ya malamulo, purezidenti amalankhula m’malo mwa dziko lanu lonse. Chimodzi modzinso, Yohane Mbatizi anapatsira machimo onse pa Yesu monga oimilira wa anthu onse.

Ndanena kuti mau onena kuti “ubatizo” ali ndi matanthauzo a uzimu monga “kutsika, kukwirira, kupatsira pa, ndi kusamutsa.” Monga mbuzi ya moyo ya Chipangano Chakale inkaphedwa pamene machimo a Israyeli anapatsidwa pa iyo, Yesu nayenso anaphedwa ndi kukwiriridwa chifukwa cha machimo athu onse omwe anapatsidwa pa Iye. 

Kunalembedwa mu Levitiko 16:21, “Ndipo Aroni aike manja ace onse awiri pamutu pa mbuzi yamoyo, ndi kubvomereza pa iyo mphulupulu zonse za ana a Israyeli, ndi zolakwa zao zonse, monga mwa zocimwa zao zonse; naike izi pamutu pa mbuziyo, ndi kuitumiza kucipululu ndi dzanja la munthu wompangiratu.” Monga ndime ikutionetsa, chaka chili chonse patsiku la chitetezero, Aroni ankaika manja ake pamutu pa mbuzi yamoyo m’malo mwa anthu onse a Israyeli malingana ndi dongosolo la oimilira, ndipo pamene iye wachotsa manja ake pamutu pa mbuzi yamoyo, machimo onse a chaka a Israyeli ankaperekedwa pa mbuzi kudzera mu manja ake monga oimilira. Anthu a Israyeli kenako ankakhululukidwa ku machimo ao onse omwe anachita chaka chonse. 

Chimodzi modzinso, chifuniro cha Mulungu pa chikhululukiro cha machimo onse a anthu chinakwaniritsidwa kudzera mu ubatizo wa Yesu. M’chipangano Chakale, mbuzi yamoyo inkalandira machimo onse a Israyeli pamene mkulu wansembe waika manja ake pamutu pake (Levitiko 16:21), pamene m’Chipangano Chatsopano, Yesu analandira machimo onse a anthu pobatizidwa ndi Yohane Mbatizi mu mtsinje wa Yordano. Nsembe zonsezi zinali nsembe za uchimo zofanana. 

Pamene Yesu ananena kwa Yohane Mbatizi, “Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero,” Iye ankanena kuti adzakwaniritsa chilungamo chonse mwa kulandira ubatizo kwa Yohane. Apa, mau onena kuti “motero” akutanthauza mwambo wa ubatizo-ndiko kunena kuti, Yohane Mbatizi wabatiza Yesu komanso Yesu walandira ubatizowu ndipo mau onena kuti “chilungamo chonse” akutanthauza kuti “moyenera” kapena “mofunika.” Mwanjira ina, pamene Yesu ananena apa, “Motero kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse,” Iye ankanena kuti kunali koyenera kwa Iye kuti alandire machimo a ali yense polandira ubatizo kwa Yohane Mbatizi. Kunena mosiyana, Ambuye wathu ankanena kwa Yohane Mbatizi, “ali yense ayenera kuponyedwa ku gahena, poti ali yense ndi ochimwa. Onse akubvutika chifukwa  cha uchimo. Ali yense akuzunzidwa ndi mdierekezi, ndipo palibe amene angadalitsidwe chifukwa cha uchimo. Choncho kwa Ine kuti ndidalitse ndi kutumiza ali yense kumwamba, ndiyenera kubatizidwa ndi iwe. Iwe uyenera kubatiza Ine m’malo mwa ali yense monga oimilira wa anthu, pakuti ndiwe mbeu ya Aroni. Tidzalandira ubatizowu kwa iwe ndipo chilungamo chonse chidzakwaniritsidwa.” Choncho pamene Yesu analamula Yohane Mbatizi kuti ambatize Iye, iye anaika manja ake pamutu pa Yesu moyenera. Pamene Yohane Mbatizi anachotsa manja ake pamutu pa Yesu, machimo onse a dziko anapatsidwa pa Yesu Kristu.

Kodi Yesu anachitapo tchimo mwa mwayi? Ai, ndithudi ai! Chfukwa Yesu anabadwa mwa Mzimu Woyera, Iye anabadwa opanda tchimo. Ndipo Iye sanachite tchimo lili lonse pamene anali mu dziko lino. Ngakhale munthu ali yense amabadwa ndi uchimo, Yesu anabadwa opanda tchimo. Ndipo Iye sanachitepo tchimo pamene anali pa dziko lino, kapena kuchita cholakwitsa chinachake.

Nanga, n’chifukwa chiani, Yesu anayenera kupachikidwa mpaka kufa? Ndi chifukwa anatenga machimo athu onse pa Iye mu mtsinje wa Yordano monga chinthu chimodzi chomwe Iye anayamba kuchita pa moyo Wake wa poyera. Kudzera mwa Yohane Mbatizi, mkulu wansembe wotsiriza wa Chipangano Chakale komanso oimilira wa mtundu onse, Yesu analandira machimo onse a munthu ali yense mu dziko lino. Ndipo pa zaka zitatu zotsatira, Yesu analalikira chipulumutso Chake ku mzinda onse wa Israyeli. Ngakhale pamene Iye anakumana ndi mkazi wogwidwa chigololo, Iye ananena kwa iye, “Inenso sindikutsutsa iwe. Sindingakuweruzenso. Ndiyenera kudziweruza ndekha. Ndiyenera kufa pamtanda m’malo mwako.”

Kuonjezerapo, pamene Yesu anapemphera m’munda wa Getsemane usiku asanapachikidwe, Iye anapempha Mulungu atate kosachepera katatu kuti chikho chakupachikidwa chimpitilire ngati nkotheka, koma chifukwa Iye anadziwa kuti chinali chifuniro cha Atate, Iye anadzibweza Yekha mu kulemekeza ndi kunena kwa Atate, “osati chifuniro change, koma chanu, chichitike.”

Kuchokera pompo mpaka pa nthawi yomwe Iye anatumizidwa kubwalo la Pilato, Yesu anazunzidwa ndi ku kwapulidwa kwambiri moonga chigawenga chachikulu moti thupi Wake lonse linang’ambika kutsala pang’ono kufa. Pamene pilato anafunsa Iye, “kodi ndiwe Kristu? Kodi ndiwe Mpulumutsi, Mwana wa Mulungu?” Yesu anati, “Ine ndine monga m’mene ukunenera. Iwe wanena wekha.” Pilato kenako anati, “ngati udzachita bwino, ndikhoza kukumasula. Ndiri ndi mphamvu imeneyo,” koma Yesu anati kwa iye, “sungakhale ndi mphamvu mwa iwe wekha pokha pokha zitapatsidwa kuchokera kumwamba,” ndipo Iye anakhala chete monga nkhonsa yokaphedwa.

Kodi n’chifukwa chiani Yesu anakhala chete monga nkhosa yokaphedwa? Ndi chifukwa choti Iye anasenza machimo athu onse, ndipo choncho iye tsopano anayenera kusenza chilango chopachikidwa m’malo mwathu, chifukwa ndi pokhapo pamene Iye akanathetsa nkhondo ya mtundu onse wa anthu, kupanga anthu onse kumasulidwa ku mazunzo a uchimo, ndi kuwapanga onse kumasuka ku ukapolo wake. Ndipo uwu ndi Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo omwe Yesu anakwaniritsa kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi pamtanda.Ambuye Anachita Chitetezero Cha Machimo Onse Adziko


Monga tidaona, Yohane 1:29 akunena kuti, “m’mawa mwace anaona Yesu ali mkudza kwa iye, nanena, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” Yohane Mbatizi, anabatiza Yesu momveka bwino kuti atetezere machimo a anthu. Patsiku lotsatira patatha ubatizo, pamene Yesu anadza kwa iye, Yohane Mbatizi ananena nati, “onani Iye! Ndi Mwanawankhosa wa Mulungu amene wachotsa machimo onse a dziko!” Yohane Mbatizi anachitira chonchi umboni za Yesu Kristu monga Mpulumutsi chifukwa iye mwini anapatsira Yesu machimo onse a anthu pombatiza Iye.

monga Yohane akuchitira umboni apa, Yesu indedi anali Mwanawankhosa wa Mulungu amene anachotsa machimo a dziko. Mwana wa Mulungu anadza pa dziko lino ndikusenza machimo onse adziko. Yohane Mbatizi ananenanso izi kachiwiri, monga kwalembedwa mu Yohane 1:35-36, “M’mawa mwacenso analikuimilira Yohane ndi awiri a akuphunzira ace; ndipo poyang’ana Yesu alikuyenda, anati, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu!”

Yohane Mbatizi ankatcha Yesu “Mwanawankhosa wa Mulungu” apa kukambaku kukuonetsa kuti monga m’mene nyama za nsembe za Chipangano Chakale zinkafera m’malo mwa anthu a Israyeli, Yesu nayenso anakhala Mwanawankhosa wathu Wansembe ndi kunyamula machimo athu onse kuperekedwa nsembe m’malo mwathu. Kunena kwina, Mwana wa Mulungu, Mlengi mwini amene anapanga ife, anadza padziko lino kupulumutsa inu ndi ine, komanso kupanga chitetezero cha machimo athu onse m’malo mwathu, Iye anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi ndi kukhetsa mwazi Wake pamtanda, motero anakhululukira machimo onse a dziko-anu ndi anga, tchimo lili lonse lochitidwa ndi ali yense lisanakhazikike dziko lapansi kufikira kumapeto a dziko, achibadwidwe komanso a tsiku ndi tsiku, posawerengera kuti ndi oipa chotani. 

Zaka 2000 zapita, Yesu anafufuta kale machimo athu onse a dziko. Mbiri inagawidwa mu AD komanso BC potengera pa chaka chomwe Yesu Kristu anadza pa dziko lino, ndi AD imodzi ikutanthauza chaka chobwera Ambuye ndipo BC ikutanthauza Yesu asanabwere. Pa 30 AD Iye anatenga machimo onse a dziko, ndipo tsopano kwatha zaka 2000 kuchokera pa nthawi ya Yesu Kristu. 

Pa 30 AD, Yesu Kristu analandira machimo onse a dziko pobatizidwa ndi Yohane Mbatizi kuti apange chitetezero cha machimo, ndipo tsiku lotsatira, Yohane Mbatizi anachitira umboni ndipo anati, “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” patapita tsiku limeneli, pamene Yohane Mbatizi anaonanso Yesu, Iye anachitiranso umboni kachiwiri nati, “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu [amene achotsa Tchimo lache la dziko lapansi]!” Yohane Mbatizi ananena za Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, kunena kuti, “Yesu wachotsa machimo anu onse. Nkhondo yanu yatha. Tsopano mulibe tchimo. Posatengera kuti ndi machimo otani mwachita, Mwana wa Mulungu wachotsa machimo onse.”

Okondedwa anzanga okhulupilira, Mulungu anakhululukira machimo anu onse potumiza Yesu pa dziko lino. Yohane Mbatizi anachitra umboni za Yesu ngati Mwanawankhosa wa Mulungu (Yohane 1:29) pamene anapatsira machimo athu onse pa Iye chifukwa iye anadza   “mwa umboni kudzacita umboni za kuunikaku, kuti onse akakhulupirire mwa Iye” (Yohane 1:7). Popanda umboni wa Yohane Mbatizi, kodi tikanadziwa bwanji ngati Yesu anachotsa machimo onse a dziko kapena tchimo la chibadwidwe lokha? Ngakhale Baibulo limanena kuti Yesu anafa chifukwa cha machimo athu, ndi Yohane Mbatizi amene ananena kuti Yesu mwini anasenza ndi kuchotsa machimo a dziko. Yohane Mbatizi anali mlatho olumikiza Chipanagano Chakale ndi Chipangano Chatsopano, ndipo iye anali kapolo wa Mulungu ofunika kuti Yesu akwaniritse Mau onse a Chipangano Chakale. Ndikupemphani inu kuti mukhulupilire mu ichi ndi kupulumutsidwa.

Yohane Mbatizi ananena za Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, ndipo iwo amene akhulupilira kuti machimo onse a anthu anapatsidwa pa Yesu mwa ubatizo Wake, ndipo kuti Iye anakhetsa mwazi Wake pamtanda ngati zotsatira, tsopano angakhulupilire mwa Yesu pa chipulumutso. Zikomo pa umboniwu wa Yohane Mbatizi, mtundu onse wa anthu ungapeze chipulumutso.

Ndikupereka kuthokoza kwanga kwa Mulungu Atate potitumizira ife Yohane Mbatizi ndi Yesu, ndi kulola Yesu kusenza ndi machimo athu onse ndikupanga chitetezero cha machimowo.