Sermons

【3-13】< Yohane 3:1-6 > Kodi Tanthauzo Leni Leni La kubadwanso Mwatsopano Ndi Chiani?< Yohane 3:1-6 >

“Koma panali munthu wa Afarisi, dzina lace Nikodemo, mkulu wa Ayuda. Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa Iye, Rabi, tidziwa kuti inu ndinu mphunzitsi wocokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kucita zizindikilo zimene Inu mucita, ngati Mulungu sakhala naye. Yesu anayankha nati kwa iye, indetu, indetu, ndinena ndi iwe, ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona Ufumu wa Mulungu. Nikodemo ananena kwa Iye, munthu akhoza bwanji kubadwa atakalamba? Kodi akhoza kulowanso m’mimba ya amace ndi kubadwa? Yesu anayankha, indetu, indetu, ndinena ndi iwe, ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa Ufumu wa Mulungu. Cobadwa m’thupi cikhala thupi, ndipo cobadwa mwa Mzimu, cikhala Mzimu. Usadabwe chifukwa ndinati kwa iwe, uyenera kubadwa mwatsopano. Mphepo iomba pomwe ifuna, ndipo ukumva mau, ace koma sudziwa kumene icokera, ndi lumene imuka; cotero ali yense wobadwa mwa Mzimu. Nikodemo anayankha nati kwa Iye, izi zingatheke bwanji? Yesu anayankha nati kwa Iye, kodi uli mphunzitsi wa Israyeli, ndipo sudziwa izi? Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, tilankhula cimene ticidziwa, ndipo ticita umboni za cimene taciona; ndipo umboni wathu simuulandira. Ngati ndakuuzani za pansi pano, ndipo simukhulupira, mudzakhupira bwanji, ngati ndikuuzani za kumwamba? Ndipo kulibe munthu anakwera kumwamba, koma Iye wotsikayo kucokera kumwamba, ndiye Mwana wa munthu, wokhala m’Mwambayo. Ndipo monga Mose anakweza njoka m’cipululu, cotero Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa; kuti yense wakukhulupira akhale nao moyo wosatha mwa Iye.”Kodi Tanthauzo La M’Baibulo Kubadwanso Mwatsopano Ndi Chiani?


Pali anthu ambiri mdziko lino omwe akuyesera kubadwanso mwatsopano pokhulupilira mwa Yesu. Koma ndiloleni kuti ndinene poyera apa kuti kubadwa mwatsopano konenedwa mu Baibulo sikudalira ntchito ya munthu. Akristu ambiri ali ndi malingaliro olakwika pa za tanthauzo la kupulumutsidwa ndi kubadwa mwatsopano. Akristu osocherawa amaganiza kuti pali ndondomeko zina zomwe ayenera kukumana nazo mwa iwo okha kuti abadwenso mwatsopano. Mwachisanzo, ena a iwo amaganiza kuti kubadwa mwatsopano, iwo ayenera kukhala moyo wao onse akudzala makachisi ambiri; ena amaganiza kuti ayenera kupita mozungulira ngati amishonale ndi kupereka myoyo yao kutsogolera maiko ena kuti akhulupilire mwa Yesu Kristu; ndipo enabe amaganiza kuti angabadwe mwatsopano ngati adzipereka okha kugwira ntchito ya Mulungu ngakhale asanakwatire. Pali Akristu osawerengeka omwe amaganiza motere masiku ano.

Zitsanzo zomwe ndapereka apazi zikungokanda pamwamba chabe. Akristu wamba amene ali ndi maganizo otere amapereka myoyo yao ku mipingo yao, kupereka chuma chao ndi kuchita ntchito zonse zopanda malipiro. Choncho amaganiza mwa iwo okha, “ngati ndingagwire ntchito molimbika chotere kwa Mulungu, Iye adzandipatsa ine mphotho ya korona wa moyo osatha. Iye adzandidalitsa ine kuti ndibadwe mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.” Pali anthu wamba ambiri amene amaganiza motere ndi kugwira ntchito molimbika mwa iwo okha kuti abadwenso mwatsopano. 

Pali zitsanzo zina za zikhulupiliro za chabe chabe mwa Akristu alero, koma chimodzi chowanda chimene onse a iwo amachita ndi kuyesa molimba kubadwa mwatsopano kudzera ku ntchito zao. Akristu ena amapereka myoyo yao kumabungwe ndi kukhuthula nthawi yao ndi mphamvu zao kuzimenezi, kuganiza, “ngati ndingatumikire Ambuye chotere, pompano Iye andidalitsa kuti ndibadwe mwatsopano.” Ena amakhala moyo wao onse m’mapemphero obwereza kupempherera ntchito zao zotumikira, ena amatumikira muzokonzakonza, ndipo ena amatumikira mumasukulu. Ngakhale Akristu ambiri amagwira ntchito za Yesu mosiyana siyana chotere, ndi zomvetsa chisoni, kuti si anthu ambiri amene akudziwa za choonadi cha kubadwa mwatsopano. Akristu otere amene amadalira pa ntchito zao zonse zabwino mwa iwo okha amaganiza kuti ngati angagwire ntchito molimbika, iwo adzabadwa mwatsopano mwa njira ili yonse. Mwachibadwidwe, ichi ndi chifukwa chake iwo akugwira ntchito molimbika njira zambiri, kuganiza kuti kugwira ntchito kwao molimbika kungapange iwo kubadwa mwatsopano.

Akristu osocherawa amaganiza kuti Mulungu adzawalola mwa njira ili yonse kuti abadwe mwatsopano monga John Wesley. Ambiri a iwo atanthauzira molakwika Yohane 3:8, yemwe akunena kuti, “Mphepo iomba pomwe ifuna, ndipo ukumva mau, ace koma sudziwa kumene icokera, ndi lumene imuka; cotero ali yense wobadwa mwa Mzimu.” Choncho amaganiza kuti munthu sadziwa pamene abadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu, ndipo kuti ngati iwo akhulupilira mwa Yesu ndi kutumikira Iye modzipereka kwambiri, posachedwapa Mulungu adzawalola kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Pali Akristu ambiri amene amaganiza mosadziwa muchikhulupiliro chao cholakwika, “ngati ndidzatumikira Ambuye modzipereka, ndidzabadwanso mwatsopano. Ndidzabadwa mwatsopano pamapeto pake ngakhale osazindikira ndekha. Tsopano ndidzagwira ntchito ya Mulungu monga okhulupilira obadwa mwatsopano, ndi kupita ku ufumu Wake pamapeto pake.”

Koma kukhulupilira motere si m’mene munthu amabadwira mwatsopano. Chifukwa chakuti munangosiya kumwa mowa, kusiya kusuta fodya, kukhala munthu wabwino, ndi kupita kumpingo mokhulupirika, izi sizikutanthauza kuti mungabadwe mwatsopano mwa njira ili yonse. Monga Ambuye wathu ananena mu ndime ya malembo alero, munthu amabadwadi mwatsopano pokhapo ngati iye “wabadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu,” ndipo zofunikira za kusinthikaku ndi madzi ndi Mzimu.

Chili chonse choposa chikhulupiliro mu Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu ndi chachabe chabe. Ngakhale Akristu ambiri amapereka ndalama zao ndi mphamvu zao kwa Ambuye ndi kugwira ntchito mwa thukuta kutsanzira Iye, ichi si chikhulupiliro chimene chingapange iwo kubadwadi mwatsopano. Kodi munthu angabadwe bwanji mwatsopano kudzera mu ndalama, kudzipereka kapena ngakhale kuphedwa? Koma Akristu ambiri amaganiza kuti zimenezi ndi zotheka. Ambiri a iwo amaganiza kuti kubadwa mwatsopano ndi chinthu chomwe munthu sangazindikire, ndipo choncho munthu amaloledwa kubadwa mwatsopano ndi Mulungu popanda kuzindikira. Amaganiza motere chifukwa zimawasitsimutsa iwo. Koma, pamene munthu wabadwadi mwatsopano, iye amadziwa za izi komanso iwo omuzungulira iye amazindikira zimenezi.

Ngakhale palibe zizindikiro zooneka kuonetsa kuti munthu wabadwa mwatsopano, ndi zoonekeratu mu Uzimu. Munthu amabadwadi mwatsopano pokhulupilira mu Mau a Mulungu amadzi, mwazi, ndi Mzimu. Izi zimazindikiridwa pamene munthu wabadwa mwatsopano. Koma, monga Nikodemo, iwo amene sanabadwe mwatsopano sangadziwe izi. Ndi chifukwa chake muyenera kumvera Mau a Yesu a chitetezero cha machimo, Mau omwe akulola inu kuubadwa mwatsopano. Ubatizo ndi mwazi wa Yesu muli chikhululukiro cha machimo chomwe chikulola ali yense kubadwa mwatsopano, ndipo pamene mudzamve Mau a Mulungu, kuphunzira ndi kukhulupilira mwa iwo, Mau a Mulungu indedi adzapanga inu kubadwa mwatsopano. Choncho, ndi chofinikira kwa inu kumvera ku Mauwa a Mulungu omwe akupanga kuthekera kwa inu kubadwanso mwatsopano.

Yesu anati mu ndime ya malembo alero, “Mphepo iomba pomwe ifuna, ndipo ukumva mau, ace koma sudziwa kumene icokera, ndi lumene imuka; cotero ali yense wobadwa mwa Mzimu.” Pamene wina amene sanabadwe mwatsopano akuwerenga ndimeyi mu Yohane 3, iye amatanthauzira ndimeyi pa iye yekha kuti azitsitsimutse yekha, kuganiza, “monga Baibulo likunena apa, palibe amazindikira pamene munthu wabadwa mwatsopano. Palibe munthu koma Mulungu Yekha amadziwa izi.” Koma umu si m’mene zilili. Mwa iwo amene anabadwa mwatsopano pokhulupilira mu Uthenga Wabwino wa Mau a choonadi, pali ena amene sadziwa kweni kweni za zimenezi. Izi ndi zotheka. Koma mu mtima mwao muli Mau a ubatizo wa Yesu ndi wazi Wake pamtanda, ndiye kuti, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo cha anthu onse. Iwo amene abadwadi mwatsopano alibe tchimo mu mtima mwao. M’malo mwake, Mau a ubatizo ndi mwazi wa Yesu, ali mu mtima mwao. Awa ndi Mau a umboni onena kuti anthu amenewa abadwadi mwatsopano. Pamene anamva Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu, iwo anazindikira kuti alibenso tchimo ndipo kuti tsopano apulumutsidwa. Ndipo anthu otere amene akhulupilira mu Mau a Mulungu a ubatizo ndi mwazi wa Yesu, Uthenga Wabwino wa chikhululukiro cha machimo onena kuti Yesu anachotsa machimo ao onse ndi madzi komanso Mzimu, apangidwa anthu a Mulungu komanso asinthidwa kukhala anthu olungama.

Koma, pamene Akristu alero afunsidwa ngati iwo abadwa mwatsopano, ambiri a iwo amanena kuti sanatero, koma pamene iwo afunsidwa ngati anapulumutsidwa, iwo amazisokoneza okha poyankha kuti anapulumutsidwa. “pamene iwo afunsidwa ngati anasinthidwa, iwo amanena kuti anatero, koma pamene afunsidwa ngati anabadwa mwatsopano, iwo amanenanso kuti sanatero. Ambiri a iwo amaganiza kuti kubadwa mwatsopano kukutanthauza kuti myoyo yao yasintha kunja, koma izo sizimene zikutanthauza kubadwa mwatsopano. Choncho Akristu oterewa samvetsetsa Mau a Uthenga Wabwino wa chikhululukiro cha machimo, Uthenga wabwino wa chipulumutso omwe umaitana ali yense kuti abadwenso mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.”

Motere, Akristu ambiri amakhulupilira mwa Yesu popanda ngakhale kuzindikira tanthauzo la Mau onena kuti ali yense ayenera kubadwa mwatsopano. Ndi chikhulupiliro chopanda pake komanso chochitsa manyazi. Koma zoona za chi Kristu cha lero ndi zakuti chikhulupiliro choterechi ndi chofala osati mwa okhulupilira wamba chabe koma ngakhalenso mwa atumiki. Chikhulupiliro chotere chakwiitsa wobadwa mwatsopano. Nanga kodi chikhulupiliro chotere chingaphwanye bwanji mtima wa Yesu, Mulungu Atate komanso Mzimu Woyera? Tiyeni tonse tsopano tibadwedi mwatsopano pokhulupilira mu Mau a ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake omwe wabweretsa chikhululukiro cha machimo ku mtundu onse wa anthu.

Ponena kuti munthu wabadwa mwatsopano, wasinthidwa, kapena kupulumutsidwa kukutanthauza chinthu chimodzi. Zoona zake, kusinthidwa kukutanthauza kupangidwanso, ndipo izi zikutanthauza kubadwa mwatsopano ngati munthu watsopano. Kunena kuti munthu wapulumutsidwa kukutanthauza kuti ngakhale munthuyu anali ochimwa poyamba, machimo ake onse anafufutidwa tsopano mokhulupilira ndi mtima onse mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu, omwe muli chikhululukiro cha machimo; ndipo Baibulo likunena kuti mtima uli onse omwe wakhulupilira m’Mau a ubatizo ndi mwazi wa Yesu wabadwa mwatsopano. Kunena kuti munthu wabadwa mwatsopano kudzera mu Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu, Mau a Mulungu kukutanthauza kuti munthu ameneyu wakhala munthu olungama, omwe mzimu wake tsopano ulibenso chili chonse chokhudza tchimo. 

Monga chonchi, Mau atatu-“ kusinthidwa,” “kukhala olungama,” komanso “kubadwa mwatsopano”-akutanthauza chinthu chimodzi. Mauwa ndi osiyana, akutanthauza chinthu chimodzi. Koma kupatula izi, Akristu ambiri amasiku ano sadziwa tanthauzo la Mau amenewo a m’Baibulo. Kunena kuti munthu wabadwa mwatsopano kukutanthauza kuti ngakhale mtima wa munthuyu wakhala uli ochimwa, koma pomvera ndi kukhulupilira mu Uthenga Wabwino wa Yesu wa madzi ndi Mzimu, iye wamasulidwa tsopano kotheretu ku machimo ake onse ndi kubadwa mwatsopano, kusinthidwa ndi kukhala munthu wolungama watsopano. Kunena kuti munthu wasinthidwa kukutanthauza kuti iye wasandulika kukhala munthu watsopano kuchokera ku ukale wake ngati ochimwa, ndipo kuti iye wakhala mwana wa Mulungu pokhulupilira m’Mau achipulumutso a madzi ndi Mzimu. Izi ndi zomwe zikutathauza ku kusinthidwa. Kunena kuti munthu wabadwa mwatsopano kukutanthauza kuti munthu wabvala ubatizo wa Yesu, kufa ndi Yesu pamodzi ndi machimo ake, ndipo kuti iye watsitsimutsidwanso. Izi zikukanba chikhulupiliro kukhulupilira kuti ngakhale munthu anali ochimwa poyamba, iye wakhala munthu olungama tsopano pomvera ndi kukhulupilira m’Mau a ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Kukamba kwina, munthu amaneyu wakhala ali ochimwa pamene iye anabadwa m’mimba mwa mayi ake, ndipo tsopano wabadwa mwatsopano kuti asandulike kukhala munthu olungama kuchokera ku ochimwa pomvera Mau a Yesu a madzi ndi Mzimu ndi kukhulupilira mu Uthenga Wabwinowu wa chikhululukiro cha machimo omwe ukulola ali yense kubadwa mwatsopano kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Munthu amaneyu angaoneke chimodzi modzi monga ali yense m’maonekedwe akunja kwake, koma mkati mwake mwabadwa mwatsopano kudzera mu Mau a ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Izi ndi zomwe zikutanthauza kubadwa mwatsopano.

Koma anthu ochepa okha amazindikira zimenezi. Ndi zamwayi ngati m’modzi mu Akristu 10,000, ndi kumvetsetsa kwathunthu pa zomwe zikutanthauza kubadwanso mwatsopano. Kodi mukundikhulupilira pamene ndi kunena kuti palibe ngakhale m’modzi mwa Akristu 10,000 abadwanso mwatsopano? Ali yense amene akudziwadi mdi kukhulupilira mu Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu angasiyanitse ngati munthu wabadwanso mwatsopano kapena ai. Inu mungachitenso zimenezi ngati mwabadwa mwatsopano mwa Mau a Yesu a madzi ndi Mzimu. Ndi Ambuye Amene Amalamulira Mphepo


Ambuye akuti, “Mphepo iomba pomwe ifuna, ndipo ukumva mau, ace koma sudziwa kumene icokera, ndi lumene imuka; cotero ali yense wobadwa mwa Mzimu.” Pamene Ambuye ananena zimenezi, Iye ankanena za ochimwa amene sanabadwe mwatsopano. Mwanjira ina, ngakhale munthu ali yense obadwa mwatsopano amadziwa tanthauzo la kubadwa mwatsopano, Nikodemo sanadziwe izi, monga iye sanadziwe komwe mphepo inkachokera komanso komwe inkapita. Mulungu amadziwa munthu ali yense amene wabadwa mwatsopano. Ndipo munthu ali yense wabadwa mwatsopano amadziwanso kuti tanthauzo la kubadwanso mwatsopano ndi chiani. Kuonjezerapo, iwo amene sanabadwe mwatsopano sadziwa tanthauzo la kubadwa mwatsopano mwa chisomo cha Mulungu, monga m’mene iwo sadziwira za komwe mphepo ikuchokera ndi komwe ikupita. 

Kodi ndani amasuntha mphepo? Ndi Mulungu. Kodi ndani amatakasa mphepo? Ndi Mulungu. Kodi Mbuye wa dziko amene amatakasa mphepo m’mwamba, kuchedwetsa ndi kutamangitsa komanso kusintha mayendedwe a mphepo ndi kuyenda kwa madzi, za moyo zonse, ndi kudzadza zolengedwa zonse ndi moyo? Ndi osaposa Yesu. Ndipo Yesu ndi Mulungu Mwini.

Koma, pokha pokha mutadziwa Mau a Uthenga Wabwino wa madzi, mwazi ndi Mzimu, Mau a chipulumutso omwe Yesu anakupatsani inu, ndiyenu simungaphunzitse ali yense. Chifukwa Ambuye wathu ananena kuti munthu amabadwa kokha mwatsopano “mwa madzi ndi Mzimu,” kuti ife tibadwe mwatsopano, tiyenera kukhulupilira mu Uthenga Wabwinowu wa chipulumutso opezeka mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu, ndi m’Mau olembedwa a Mulungu. Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu uli ndi mphamvu zodabwitsa zomwe zimapangitsa ali yense kubadwab mwatsopan.

Mzimu Woyera ndi “pneuma” mu chi Greek, kuchokera ku mneni wa chi Greek “pneho” omwe akutanthauza kuti “kupuma kapena kuuzilira mphepo.” Mzimu Woyera umalowa mu mtima mokhamo mwa iwo amene akhulupilira mu Mau Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu operekedwa ndi Yesu. Pamene Yesu anabatizidwa kuti apange chitetezero cha machimo onse a anthu, Iye anachotsa machimo onse a dziko, ndipo anaweruzidwa m’malo mwathu chifukwa cha machimo athu, Iye anakhetsa mwazi Wake pamtanda, motero anakwaniritsa chipulumutso chopanga ali yense kubadwa mwatsopano. Ndi m’mitima ya iwo amene akhulupilira m’Mauwa momwe Mzimu Woyera umalowa. Ichi ndi chipulumutso chobadwa mwatsopano chosindikizidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo iwo amene machimo ao anasenzedwa ndi Yesu abadwa mwatsopano.

Genesis 1:2 akuti, “dziko lapansi ndipo linali lopanda kanthu; ndipo mdima unali pamwamba pa Nyanja; ndipo Mzimu wa Mulungu unalinkufungatira pamwamba pa madzi.” Kunalembedwa kuti Mzimu wa Mulungu unalinkufungatira pamwamba pa madzi. Izi zikutanthauza kuti Mzimu wa Mulungu unalinkufungatira pamwamba pa dziko lapansi. Ndimeyi ikutanthauza kuti Mzimu wa Mulungu sungadze mu mtima mwa ali yense amene ali ndi tchimo. Iwo amene sanabadwe mwatsopano ali ndi mtima wosokonezeka, ali ndi tchimo mkati mwao, ndipo choncho ali ndi mdima mwa iwo. Pa chifukwa icho, Mzimu Woyera sungakhale mu mtima mwa ali yense ochimwa. Choncho Mulungu anaunika mtima wa munthu wosokonekerawu ndi opanda kanthu ndi Uthenga Wabwino wakuunika wa Mau Ake, omwe ukupanga kuthekera kuti ali yense abadwenso mwatsopano. Pamene Mulungu anati kuyere, kunayera ndipo pokhapo ndi pamene Mzimu wa Mulungu unapezeka ndi munthu mkati mwake. Choncho anthu obadwa mwatsopano amene akhulupilira m’Mau a Uthenga Wabwino wa Yesu wa madzi ndi Mzimu ali ndi Mzimu Woyera mu mitima yao. Umu ndi m’mene iwo anabadwira mwatsopano. Iwo anabadwa mwatsopano pomvera ndi kukhulupilira mu Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu, omwe ndi, Mau a chipulumutso omwe Yesu anawapatsa iwo. 

Kodi munthu amabadwa bwanji mwatsopano? Pofuna kukamba nkhani iyi, Ambuye wathu ananena kwa Nikodemo, Mfarisi, “munthu ayenera kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.” Nikodemo kenako anafunsa Iye, “kodi munthu angabadwe bwanji mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu? Kodi iye ayenera kubwerera m’mimba mwa mayi wake kachiwiri?” posamvetsetsa chili chonse, Nikodemo anatenga mwa Mau chabe pamene Yesu anamuuza iye za kubadwa mwatsopano, n’chifukwa chake iye anafunsa Yesu ngati munthu ayenera kubwereranso m’mimba kachiwiri. Pamene Yesu ananena kwa iye, “kodi sudziwa izi ngakhale uli mphunzitsi wa a Israyeli?” choncho Yesu ananena kwa Nikodemo kuti ngati munthu sabadwa mwatsopano, sangaone ufumu wa kumwamba kapena kulowamo. Mwatsatanetsatane, Yesu kenako anafotokozera Nikodemo Mfarisi choonadi cha kubadwa mwatsopano. 

Zoona za lero ndi zakuti pali Akristu ambiri mu dziko lino amene sanabadwe mwatsopano ngakhale amakhulupilira mwa Yesu. Akristu wamba otere akupezeka mu manambala a akulu pakati pa anthu odziwika bwino. Iwo onse apa ali monga Nikodemo Mfarisi. Nikodemo anali monga mtsogoleri wa Akristu muchilankhulo cha lero, monga bishop kapena mtsogoleri wa sinodi kapena mpingo. Ndipo mu zakunja, iye anali mtsogoleri wa chipani, chimodzi modzi ndi mkulu wa nyumba ya malamulo lerolino. Kuonjezerapo mukukamba kwa chipembedzo, iye anali mphunzitsi wa chi Yuda. Iye anali mtsogoleri wa chi Yuda amene anakhulupilira mwa Mulungu. Iye anali ophunzira kwambiri ku zonse za kuthupi ndi zaumulungu. Mu masiku amenewo Israyeli analibe masukulu ogawikana; m’malo mwake ali yense ankaphunzira m’masunagogi wamba. Munthu ali yense amene waphunzira kwambiri m’mzindawo ankaphunzitsa m’masunagogi, ndipo monga munthu uyu, Nikodemo anali m’modzi wa aphunzitsi odziwika wa Israyeli. Koma posawerengera kudziwika kwake, Nikodemo anali asanamve za kubadwanso mwatsopano. Mwachidule, iye anali mphunzitsi wabodza. Motere mu masiku anonso, pali atsogoleri ambiri a chiKristu abodza. Atsogoleri abodzawa sanabadwe mwatsopano iwo okha, ndipo iwo akuphunzitsabe owatsatira ao amene, monga iwo, sanabadwe mwatsopano. 

Pali Akristu ambiri a zaumulungu, aphunzitsi, madikoni, akulu a mpingo, atumiki, azibusa ndi mabishopu mu dziko lino, amene sanabadwe mwatsopano. Anthu amenewa sadziwa kuti munthu angabadwe bwanji mwatsopano pokhulupilira mwa Yesu. Monga Nikodemo, ambiri a iwo amaganiza kuti munthu ayenera kulowanso m’mimba mwa mayi wake kachiwiri ndi kubadwanso mwatsopano. Iwo amadziwa bwino kuti iwo okha ayenera kubadwanso mwatsopano, koma ndi mbuli za Mau a Mulungu ndipo sadziwa kuti ndi Mau otani a Yesu omwe ayenera kubadwa nao mwatsopano. Chifukwa azibusa otere ndi opanda kanthu, iwo amangokamba za chuma cha dziko chomwe amachimva ndi kuganiza m’maulaliki ao, monga munthu wa khungu amene amyesera kukamba za njobvu mwakuigwira. Ichi ndi chifukwa chake pali Akristu ambiri amene sanabadwe mwatsopano. 

Si mwa ntchito zanu, pochita china chake mwa inu nokha, kuti mungabadwe mwatsopano pamaso pa Mulungu. Koma, mwabadwa mwatsopano chifukwa cha Mulungu, chifukwa Iye wapanga kuthekera kwa inu kuti mubadwe mwatsopano ngati munthu olungama kuchokera ku ochimwa kudzera mu Mau a Uthenga Wabwino wa madzi, mwazi, ndi Mzimu. Yesu ananena kwa Nikodemo, “ngati ndakuuzani za pansi pano, ndipo simukhulupira, mudzakhulupira bwanji, ngati ndikuuzani za kumwamba?” anthu ambiri sakhulupilira kuti ubatizo wa Yesu muli choonadi chomwe chimakhululukira mphotho ya machimo ao. Kodi ndi chiani chomwe iwo sakhulupilira? Iwo sakhulupilira mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo omwe Yesu watipatsa ife kuti tibadwe mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Iwo amene sanabadwe mwatsopano sakhulupilira ngakhale pamene auzidwa za pansi pano, ndipo kodi iwo angakhulupilire bwanji pamene obadwa mwatsopano awauza iwo za ntchito ya kumwamba ya kubadwa mwatsopano? Izi ndi zomwe Yesu ankatanthauza pamene Iye anauza Nikodemo, “ngati ndakuuzani za pansi pano, ndipo simukhulupira, mudzakhulupira bwanji, ngati ndikuuzani za kumwamba?” pofufuta machimo a ochimwa ali yense ndi kutsuka machimowo, Yesu mwini anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi pa thupi lake, kufa pamtanda, kuukanso kwa akufa, ndipo motero kupanga kuthekera kwa ochimwa onse kubadwanso mwatsopano. Choncho Yesu akufunsa ochimwa, “ndakupulumutsani inumwa madzi ndi Mzimu, koma kodi mudzakhulupilira mwa Ine ngati ndakuuzani za kumwamba izi?”

Ambuye wathu kenako anagwiritsa ntchito Chipangano Chakale kudzifotokoza Yekha kwa Nikodemo ndi kunena kwa iye, “Ndipo kulibe munthu anakwera kumwamba, koma Iye wotsikayo kucokera kumwamba, ndiye Mwana wa munthu, wokhala m’Mwambayo. Ndipo monga Mose anakweza njoka m’cipululu, cotero Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa; kuti yense wakukhulupira akhale nao moyo wosatha mwa Iye.” Yesu anati monga Mose anakweza njoka ya nkuwa m’chipululu, kotero mwana wa munthu ayeneranso kukwezedwa kuti yense okhulupilira mwa Iye akhale nao moyo osatha.

Kodi chomwe Ambuye wathu akutanthauza ndi chiani pamene Iye akuti, “monga Mose anakweza njoka m’cipululu, cotero Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa”? Ambuye wathu anachokera ku Chipangano Chakale kuti afotokoze bwino Mau opatsidwa a Mulungu a chitetezero cha machimo, Mau a chipulumutso okwaniritsidwa ndi Ambuye wathu kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi. Kuti Ambuye wathu apachikidwe mpaka kufa- ndiko kuti, kukwezedwa kumwamba-Iye choyamba anayenera kulandira machimo a ochimwa onse adziko kudzera mu ubatizo omwe Iye analandira kwa Yohane Mbatizi. Monga Yesu analibe tchimo kuchokera pachiyambi, Iye sakanapachikidwa pamtanda otembeleredwa. Kuti Ambuye wathu apachikidwe ndi kupanga chitetezero cha machimo onse kwa ali yense ochimwa mu dziko lino, Iye anayenera kubatizidwa poyamba. Choncho, chifukwa cha chitetezero cha machimo onse a anthu, Yesu analandira machimo onse kudzera mu ubatizo Wake, ndipo kuti atembeleredwe chifukwa cha machimo onsewa a dziko, Iye anapachikidwa ndi kukhetsa mwazi Wake mpaka kufa. Pokhapo kenako Iye akanapulumutsa ochimwa ali yense ku tchimo lili lonse. Munjira iyi, Yesu anabweretsa chipulumutso kwa ochimwa onse kuti iwo abadwenso mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.

Nikodemo anali odziwa bwino m’Chipangano Chakale. Pamene Yesu anauza iye kuti, “cotero Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa; kuti yense wakukhulupira akhale nao moyo wosatha mwa Iye.” Iye ankauza iye choonadi cha kubadwa mwatsopano, kuti polandira machimo onse a dziko mwa kubatizidwa ndi Yohane Mbatizi, Iye akanapulumutsa ochimwa onse ku machimo a dziko mwa kukhomeredwa pamtanda. Mwa njira ina, awa anali Mau a Mulungu onena kuti Yesu Kristu anali Mesiya ndi Mpulumutsi, amene Iye anayenera kufa pamtanda chifukwa cha ubatizo Wake, ndipo kuti ali yense wakhulupilira mwa Yesu monga Mpulumutsi Wake angabvale ubatizo Wake ndipo choncho kufa ndi Kristu ndi kuuka kwa akufa pamodzi Naye. Pa mbuyo Pake, Nikodemo anamvetsetsa tanthauzo la Mauwa. Monga Njoka Ya Nkuwa Inakwezedwa M’mwamba Pa Mtengo 


Kodi mukukumbukira ku Chipangano Chakale m’mene Mose anakwezera njoka ya nkuwa pantengo m’chipululu? Numeri 21 ananena kuti pamene anthu a Israyeli anali kuyenda m’chipululu atachoka ku Aigupto, iwo anakhumudwitsidwa ndi nyengo zowawa zomwe anakumana nazo. Choncho anadandaulira mtsogoleri wao Mose ndi Mulungu, ndipo pa tchimo limeneli Mulungu anatuma njoka zamoto kwa iwo ndi kuthira nkwiyo wake pa iwo. Njoka za moto zinaluma a Israyeli m’chipululu, ndipo sipanatenge nthawi yaitali ambiri a iwo anayamba kufa kuchoka tubvu kukamwa ndi mathupi ao kutupa.

Koma, pamene mose anaona anthu ake akufa mululu kukulumidwa kwa njoka, iye anapemphera kwa Mulungu monga mtsogoleri wao, kunena kuti, “Ambuye, chonde pulumutsani anthuwa.” Mulungu kenako anauza Mose kuti apange njoka ya nkuwa ndi kuika pamtengo, ndikufuula kwa anthu kuti ali yense oyang’ana njoka ya nkuwa pamtengo adzakhala ndi moyo. Mose kenako anauza anthu a Israyeli zomwe Mulungu ananena kwa Iye. Kwa a Israyeli amene anakhulupilira mwa mau a mtsogoleri wao Mose ndi kuyang’ana pa njoka ya nkuwa, ululu wa njoka zamoto unachoka kwa iwo. Izi zikutanthauza kuti monga munthu analumidwa ndi satana, ululu wa tchimo uyenera kuchotsedwa kwa iye. Pamene anthu a Israyeli anakhulupilira mu mau a Mose ndi kuyang’ana pa njoka ya nkuwa pamtengo, iwo anapulumutsidwa. 

Kunena kuti Mose anakweza njoka m’mwamba pamtengo zikutanthauza choonadi choti ngakhale satana amatakasa munthu ali yense kuchita tchimo ndi kupatsa mlandu Mulungu chifukwa cha izi, Ambuye wathu anasenza matembelero onse a ochimwa pobatizidwa, ndipo Iye anapanga chitetezero cha machimo onsewa ndi kutsriza tembelero lili lonse mwa kupachikidwa mpaka kufa. Polumidwa ndi njoka ya kale ya satana, ife tonse anthu tinayenera kuphedwa ndi kutembeleredwa, koma pofuna kupulumutsa anthu otere monga ife ndi kupanaga chitetezero cha machimo onse a ali yense mu dziko lino, Ambuye anasenza machimo onse a munthu ali yense ochimwa mwa kubatizidwa, anapachikidwa mpaka kufa, kuukanso kwa akufa, ndipo motero anapulumutsa okhulupilira Ake onse.

 M’Chipangano Chakale nkani ya njoka ya nkuwa yomwe taona, ali yense wayang’ana pa njoka ya nkuwa pamtengo anapulumutsidwa. Chimodzi modzinso, tsopano mu nthawi ino ya Chipangano Chatsopano, monga Yesu Kristu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi ndi kupachikidwa kupanga chitetezero cha machimo onse adziko Mulungu wapereka madalitso ya kubadwa mwatsopano kwa ali yense amene akhulupilira mwa Kristu ngati Mpulumutsi wake komanso mwa ubatizo Wake ndi mwazi ngati chipulumutso chake. Ambuye wapanga chitetezero cha machimo onse a dziko lino mwa kubatizidwa ndi Yohane Mbatizi mu mtsinje wa Yordano ndipo motero asenza machimo onse Payekha, komanso mwa kupachikidwa ndi kukhetsa mwazi Wake pamtanda. Iye motero wapulumutsa ali yense amene wakhulupilira ndi mtima wake onse mu madzi Ake ndi mwazi ngati chipulumutso chake. 

Yesu anati, “ndipo kulibe munthu anakwera kumwamba, koma Iye wotsikayo kucokera kumwamba, ndiye mwana wa munthu, wokhala m’Mwambayo.” Ambuye wathu anatsegula zipata za kumwamba mwa kubatizidwa ndi kukhetsa mwazi Wake kupereka mphotho ya machimo. Kunalembedwa, “Ine ndine njira, ndi coonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine” (Yohane 14:6). Monga Ambuye wathu anatenga machimo onse a anthu mwa kubatizidwa ndikutsegula zipata za kumwamba za chipulumutso mwa kupachikidwa, Iye wapulumutsa kumachimo onse ali yense ameme akhulupilira mwa Yesu Kristu monga Mpulumutsi wake. Iye wapereka mphotho ya machimo Payekha kuti ali yense wakhulupilira mu choonadi cha madzi, mwazi ndi Mzimu angalowe ufumu wa kumwamba. Ndi kudzera mu Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu omwe Ambuye apulumutsa anthu onse. Chomcho, kunena kuti munthu wabadwa mwatsopano kukutanthauza kuti munthuyu ali ndi chikhulupiliro mu ubatizo wa Yesu, mwazi Wake, komanso Umulungu Wake.

Kodi Yesu anatanthauza chiani pamene Iye ananena kuti, “monga Mose anakweza njoka m’cipululu, cotero Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa”? kodi panali chifukwa china chomwe Ambuye wathu anayenera kupachikidwa? Kodi Iye anachitapo tchimo monga ife? Kodi Iye anali ofooka monga ife? Kodi Iye anachita zolakwa monga ife? Ai, nditudi ai. Nanga n’chifukwa chiani Ambuye wathu anayenera kupachikidwa pamtengo otembeleredwa wapamtanda? Kunali kupanga chitetezero cha machimo onse a dziko, anu ndi anga pamodzi, ndi kupulumutsa komanso kuombola onse amene akhulupilira mwa Yesu ku machimo ao onse ndi kukhetsa mwazi Wake pamtanda.

Yesu Kristu anapulumutsa onse a ife amene takhulupilira mu madzi Ake komanso mwazi ngati chipulumutso chathu ku machimo. Chifukwa Ambuye anasenza machimo anu onse ndi machimo anga Payekha mwa kubatizidwa mu mtsinje wa Yordano, Iye anayenera kupachikidwa pamtengo otembeleredwa wamtanda; ndipo pamene Iye anasenza machimo onse a dziko kudzera mu ubatizo Wake, kunyamulira machimowo pamtanda, ndi kupachikidwa kukhetsa mwazi Wake pamtanda, Iye wapulumutsa ife tonse. Choncho awa ndi mau a chikhululukiro cha machimo omwe atipanga ife kubadwa mwatsopano mu moyo watsopano monga iwo okhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake ngati chipulumutso chathu ndi chitetezero cha machimo athu.

Baibulo likunena poyera kuti munthu amabadwa mwatsopano pamene iye wakhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pamtanda. Ndi kukhulupilira mu Mau olembedwa a Mulungu a madzi, mwazi, ndi Mzimu-ndipo kunena kuti, mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo-kuti takhala ana a Mulungu. Mu Baibulo, madzi apa akutanthauza ubatizo wa Yesu (1 Petro 3:21) ndipo Mzimu ukutanthauza kuti Yesu ndi Mulungu mwini, ndipo awa ndi Mau omwe munthu amabadwa mwatsopano, kunena kuti Yesu wapulumutsa ochimwa onse pobwera pa dziko lino mwa thupi la munthu, kulandira machimo onse a mtundu wa anthu pobatizidwa ndi Yohane Mbatizi, ndi kukhetsa mwazi Wake pamtanda, zonse pofuna kukwaniritsa chipulumutso cha uzimu cha anthu ndi chitetezero cha machimo athu. Pamene thupi la Yesu Kristu linabatizidwa ndi kusenza chilango chonse cha machimo a anthu pamtanda, Yesu Kristu anapulumutsa okhulupilira Ake onse ku machimo onse a dziko. Tiyenera kukhulupilira kuti ubatizo wa Ambuye ndi mwazi muli chipulumutso cha ochimwa onse ndi chikhululukiro cha machimo onse. Izi ndi zomwe ankatanthauza pamene Iye ananena kuti okhawo amene abadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu angaone ndi kulowa ufumu wa Mulungu. Ambuye wathu wapulumutsa inu ndi ine kudzera mu madzi a ubatizo Wake, mwazi Wake ndi Mzimu. Kodi mukukhulupilira mu zimenezi?

Ambuye wathu ndi “Mkulu Wansembe wa ufumu wa kumwamba,” ndipo pofuna kupanga chitetezero cha machimo a mtundu wa anthu mu dziko lino, Mkulu Wansembe wa kumwamba anabatizidwa pa dziko lino, kukhetsa mwazi Wake mpaka kufa pamtanda, kuukanso kwa akufa, ndipo motero kupulumutsa onse amene akhulupilira mwa Kristu moonadi. Iye motero wakhala Mpulumutsi wa okhulupilira Ake onse.

Ambuye wathu ndi “Mkulu Wansembe wa ufumu wa kumwamba,” ndipo pofuna kupanga chitetezero cha machimo a mtundu wa anthu mu dziko lino, Mkulu Wansembe wa kumwamba anabatizidwa pa dziko lino, kukhetsa mwazi Wake mpaka kufa pamtanda, kuukanso kwa akufa, ndipo motero kupulumutsa onse amene akhulupilira mwa Kristu moonadi. Iye motero wakhala Mpulumutsi wa okhulupilira Ake onse. 

Ambuye ananena mu Yohane 10, “Ine ndine khomo la nkhosa.” Ambuye waima pa chipata cha kumwamba. Kodi ndindani amene amatsegula zipata za kumwamba? Ndi Ambuye wathu amene amatsegula. Kuchitira kwa onse amene akhulupilira mwa Iye, Ambuye anabatizidwa pa dziko lino, kukhetsa mwazi Wake, ndi kuukanso kwa akufa. Iye wapulumutsa kumachimo ali yense amene wakhulupilira ndi mtima onse mu ntchito yake ya chipulumutso. Ndipo Iye watsegula zipata za kumwamba kwa onse amene akhulupilira mu chipulumutso cha madzi Ake ndi mwazi kuti alowe mkati. Koma, Iye watembenuza nkhope Yake kwa ochimwa amene, posawerengera kukhulupilira kwao mwa Yesu, sadziwa bwino bwino m’mene Iye anachotsera machimo ao, komanso amene chikhulupiliro chao motero ndi cholakwika. Akristu osocherawa sanabadwe mwatsopano pakuti iwo sakhulupilira mu ubatizo Wake, mwazi Wake, ndi Mzimu; iwo sakhulupilira mwa Yesu malingana ndi Mau; ndipo iwo amakana Umulungu Wake ndi kunyalanyaza kubvomera kuti Yesu ndi Mulungu mwini. Ambuye wayang’ana kumbali kwa anthu otere. Ndipo Ambuye waweruza kuchionongeko onse amene akana Mau olembedwa a Mulungu komanso chisomo Chake cha chipulumutso-ndiye kuti, iwo amene akana kuti Yesu anachita chitetezero cha machimo onse a anthu pobatizidwa ndi kukhetsa mwazi Wake pamene Iye anadza pa dziko lino mu thupi la munthu, kuti Iye anauka kwa akufa mu masiku atatu, ndipo kuti Iye kenako anakwera kumwamba. Mwachidule, ali yense amene sakhulupilira mwa Yesu ameneyu monga Mpulumutsi wake adzaonogedwa, pakuti Baibulo limati, “mphotho yace ya ucimo ndi imfa.”

Kuonjezerapo, iwo amene mitima yao yakhala yopanda uchimo pokhulupilira mu chipulumutso chomwe Ambuye anabweretsa-ndiko kuti, iwo amene akhulupilira kuti Yesu anadza pa dziko lino ndi kupanga chitetezero cha machimo ao onse pa kubatizidwa ndi kufa m’malo mwao-adalitsidwa ndi Ambuye kulowa kumwamba. Uthenga Wabwino umenewu wa chitetezero cha machimo omwe wapanga kuthekera kwa onse kuti abadwe mwatsopano ndi osaposa Uthenga Wabwino onena kuti Yesu anadza mwa madzi, mwazi ndi Mzimu. Uthenga wabwino wa madzi ndi mwazi ndi Uthenga Wabwino wa choonadi omwe wapanga inu kubadwa mwatsopano. 

Monga anthu a Israyeli anapulumutsidwa kuchokera ku imfa pamene anayang’ana pa njoka ya nkuwa yomwe inaikidwa pamtengo m’chipululu, pamene Ambuye wathu anadza pa dzikolino, Iye anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi ndikukwezedwa pa mwamba pamtanda ku chikhululukiro cha machimo, ndipo Iye anasenza chilango ndi chiweruzo cha tchimo lili lonse la munthu pokhetsa mwazi Wake chifukwa cha ife. Yesu Kristu motero anapanga kuthekera kwa ali yense kuti apulumutsidwe pokhulupilira muchipulumutsochi chomwe anabweretsa ku mtundu wa anthu. Ndi mwa Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo omwe munthu amabadwa nao mwatsopano. Uthenga Wabwino wa choonadi umenewu ndi njira ya choonadi ya chipulumutso kwa inu ndi ine, komanso chioombolo cha mtundu onse wa anthu. Kodi mukukhulupilira mu zimenezi? Pamene Yesu ananena kuti munthu ayenera kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu, Iye ankakamba za Uthenga Wabwino wa kumwamba wa kusinthika. Kunena kuti munthu wabadwa mwatsopano, wasinthika, wakhala watsopano, kupulumutsidwa ndi kupangidwa popanda tchimo kukutanthauza kuti munthuyu wakhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pamtanda. Ali yense amene wakhulupilira mu Uthenga Wabwinowu wa madzi, mwazi, ndi Mzimu alibe tchimo. Ndi anthu otere amene abadwa mwatsopano.

Koma, chokwiitsa choonadi lerolino ndi chakuti pafupi fupi ali yense mu dziko lino, kuphatikiza a Kristu onse, sadziwa choonadi ichi monga m’mene Nikodemo sanadziwe pachiyambi. M’mau a dziko, Nikodemo anali munthu wa mkulu. Iye anali membala wa bwalo la milandu. Apa mu Yohane 3:15, Baibulo likunena za nkhani yomwe Yesu anali nayo ndi Nikodemo. Pambuyo pake, pamene Yesu anapachikidwa mpaka kufa, Nikodemo anadza ndi kukwirira thupi la Yesu. Iye anapita kwa Pilato ndi kumpempha iye thupi la Yesu, kuti iye apereke maliro oyenera, ndipo iye anamkwirira Iye mu manda opanga omwe Yosefem wa ku Arimathea anakonza yekha.

Kudzera mu madzi Ake a ubatizo, mwazi Wake pamtanda, imfa Yake yomwe anabvutika kulipilira mphotho ya machimo, komanso kuuka kwake, Ambuye wathu Yesu watipatsa ife Uthenga Wabwino wa choonadi omwe watipanga ife kubadwa mwatsopano mwa chikhulupiliro. Koma, pali Akristu ochepa amene akudziwa choonadi ichi cha kubadwa mwatsopano m’maofesi onse a mipingo moti m’modzi mwa anthu 1,000, kapena m’modzi mwa anthu 10,000, ndi omwe akudziwa izi. Anthu ambiri m’nyengo ino sadziwa choonadi cha madzi a Yesu ndi Mzimu. Ili ndi tsoka lokuswa mtima. Yesu watidalitsa ife kuti tibadwe mwatsopano, Iye wapanganso kuthekera kwa ali yense mu dziko lino kubadwa mwatsopano. Kodi ndi chiani chimene timakhulupilira, chomwe Ambuye watidalitsa nacho ife kuti tibadwe mwatsopano? Timakhulupilira m’madzi, mwazi ndi Mzimu-ndiko kuti, timakhulupilira kuti Ambuye anasenza machimo athu pamene Iye anabatizidwa, kufa pamtanda kulipira mphotho ya machimo onsewa, ndi kuuka kwa akufa-ndipo ndi mwachikhulupilirochi chomwe Ambuye watipatsa ife moyo wa tsopano kuti tibadwenso mwatsopano. Yesu ndi Ambuye wachipulumutso amene wadalitsa onse okhulupilira onse kuti abadwenso mwatsopano mwa madzi a ubatizo Wake komanso mwazi Wake. Choncho ndi kupempha onse a inu kuti mukhulupilire mwa Ambuye ameneyu, Mlengi wa kumwamba ndi dziko komanso chilengedwe chonse, ndi kukhala mwa Iye kwa muyaya.

Yohane 3:16 akuti, “Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana Wace wobadwa Yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.” Talandira moyo osatha mwa kukhulupilira mwa Ambuye wathu Yesu. Tabadwa mwatsopano pokhulupilira m’madzi a Ambuye ndi Mzimu. Pokhulupilira mu Uthenga Wabwino wa choonadiwu, omwe Ambuye watipulumutsa ife kudzera mu Mau a madzi ndi Mzimu, tabadwanso mwatsopano. Zoonadi, ali yense angapulumutsidwe ngati Iye akhulupilira mu Uthenga wabwinowu wa chipulumutso, Uthenga Wabwino wa madzi ndi mwazi operekedwa ndi Yesu, ndi kukhulupilira kuti Yesu ndi Mulungu mwini komanso Mpulumutsi; koma ngati iye satero, ndiye kuti iye adzaponyedwa ku gahena kwamuyaya. Kuti Yesu, Mlengi Mwini, anadza pa dziko lino mu thupi la munthu, anabatizidwa, kufa pamtanda, ndi kuuka kwa akufa-ntchito imeneyi ya chipulumutso yapanga kuthekera kwa ali yense kubadwa mwatsopano, ndipo izi ndi zomwe Yesu anachita kwa ife. Ndipo ichi ndi chifukwa chake Ambuye wathu ananena kwa Nikodemo, “ngati ndakuuzani za pansi pano, ndipo simukhulupira, mudzakhulupira bwanji, ngati ndikuuzani za kumwamba?”

Okondedwa okhulupilira anzanga, kodi chomwe Mulungu wachita kwa ife anthu ndi chiani? Iye wachita ntchito ya chipulumutso, pakuti Yesu Mulungu oonadi anadza mwa Yekha pa dziko lino mu thupi la munthu, anabatizidwa ndi kulandira machimo onse kudzera mu ubatizo Wake, anapereka thupi Lake kuchiweruzo pamtanda ndi kufa, kuuka kwa akufa, ndipo motero wakhala Mpulumutsi wa muyaya kwa onse okhulupilira mwa Iye. Monga m’mene zilili Yesu amene analenga dziko lonse ndi chili chonse m’menemo, choncho ndi Ambuye amene wapulumutsa ndi kuombola myoyo yathu yonse ku machimo. Uwu ndi Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu omwe ukupanga ife kuthekera kuti tibadwe mwatsopano. Ntchito imeneyi yomwe yapanga ali yense kubadwa mwatsopano ndi chipulumutso chomwe chinakwaniritsidwa mwa Yesu. 

Yesu anapulumutsa inu ndi ine ku dziko losokonekera, ku machimo ake, komanso kuzokwawa za mdierekezi. Iye wapulumutsa okhulupilira ake onse ku machimo ndi chiweruzo pobwera pa dziko lino ndi kuombola ochimwa onse, kubatizidwa kuti atenge machimo adziko lapansi, kuwanyamulira machimowo pamtanda ndi kufa, komanso ndi kuuka kwa akufa. Kukhulupilira mu izi ndi kugwira ntchito ya Mulungu. Ndi mwa kukhulupilira muchipulumutsochi cha madzi ndi mwazi kuti munthu angapulumutsidwe ndi kubadwa mwatsopano. 

Mulungu akunena kuti pali mitundu iwiri ya chisomo yomwe anakhuthulira pa anthu: chimodzi ndi chisomo chapadera, ndipo ndi chisomo cha onse. Chisomo cha onse chikutanthauza madalitso amene Mulungu anapereka mofanana kwa ali yense-mwachitsanzo, dzuwa lomwe timasangalala nalo, mpweya omwe timapuma, mitengo ndi zina zonse zolengedwa zomwe tikuona, chakudya chomwe timadya, ndi zina zotero. Madalitso amenewa amachedwa chisomo cha onse chifukwa Ambuye anakhuthulira pa ali yense, anthu ochimwa ndi olungama pamodzi. Kodi chisomo chapadera ndi chiani? Ndi madalitso a chipulumutso kuti pamene tinali kuonongeka mu uchimo, Mulungu mwini anadza pa dziko lino kupulumutsa ife ku machimo, ndipo kudzera mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu, kwapanga kuthekera kuti ife tibadwe mwatsopano.Chisomo Chapadera Cha Mulungu


Yohane 3:16 akutanthauza za chisomo chapadera cha Mulungu, kunena kuti, “Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana Wace wobadwa Yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.” Chisomo chapaderachi cha Mulungu ndi chosaposera chilungamo choti Yesu anadza pa dziko lino mu thupi la munthu ndi kufufuta machimo athu onse mwa kubatizidwa ndi kupachikidwa. Ichi ndi chipulumutso ku machimo onse, chomwe ndi choonadi ndi moyo, ndi ndendende chipulumutso chapadera cha Mulungu. Zomwe Yesu wachita kwa ife, kuti Iye wapulumutsa ife ochimwa, ndi chisomo chapadera cha chipulumutso, ndipo pokhapo pamene takhulupilira mu choonadi ichi tadalitsidwa kuti tibadwe mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu ndi kupeza chipulumutso chathu mwa chisomo chapadera cha Mulungu.

Ndi cholakwika choopsa kuti m’Kristu ali yense mu dziko lino akane chisomo chapederachi cha Mulungu ndipo m’malo mwake kukakamila kukhala moyo wa chi Kristu. Chikhulupiliro chotere ndi cha chabe. Onse a ife tinganene kapena mtsogoleri wa a Kristu anabadwadi mwatsopano kapena ai pongowerenga chimodzi mwazolemba zake. Ndapereka maulaliki osawerengeka, koma mulibe ulaliki omwe ndinalephera kulalika za kubadwa mwatsopano kudzera m’Mau a ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Pali ponse pomwe ndatsegula Baibulo kuchokera ku Genesis kufikira ku Chibvumbulutso, mathero anga nthawi zonse amafika ku chisomo cha Mulungu, madalitso apadera a kubadwa mwatsopano omwe Yesu watipatsa ife. Izi zili chonchi chifukwa chomwe chimaonetsa chisomo cha Mulungu cha chipulumutso ndi chipulumutso chomwe Yesu anabweretsa kwa ochimwa onse kudzera mu ubatizo ndi mwazi Wake pamtanda.

Ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pamtanda muli chisomo chapadera cha Mulungu. Koma, azibusa abodza a dziko lino satsatira Mauwa a chisomo chapadera cha Mulungu. Koma abodza amenewa azipanga okha ngati angelo a kuunika, kunamizira kugwira ntchito ngati akapolo achilungamo ankhondo a chipembedzo komanso makhalidwe a anthu. Indedi, ngakhale amachita zodabwitsa ndi kuchiza odwala, zinthu zonsezi ndi ntchito zoipa zomwe zili kutali ndi chisomo chapadera cha Mulungu.

Okondedwa anzanga okhulupilira, tonse tinali ochimwa mwachilengedwe, koma Ambuye watitsa ife Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, ndipo chosaposa ichi ndi chisomo chapadera cha Mulungu. Mwa chisomo chake chapadera Ambuye wadalitsa onse okhulupilira Ake kuti abadwenso mwatsopano. Ngakhale tinali ochimwa kufikira ku imfa, Mulungu wadalitsa ife kuti tikhale anthu atsopano komanso ana Ake kudzera mu madzi Ake, mwazi, imfa ndi kuuka. Ichi ndi chisomo cha Mulungu chomwe chapanga ali yense okhulupilira kukhala munthu olungama komanso opanda tchimo. Kodi mumakhulupilira izi? Kodi izi zinachitikanso kwa inu? Ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, imfa ndi kuuka ndi zomwe zikupanga chisomo chapadera cha Mulungu chomwe Ambuye anatipatsa kudzera m’Mau a madzi ndi mwazi. Uwu ndi Uthenga Wabwino wa chisomo chapadera cha Mulungu. Ndikuthokoza Ambuye wathu potipulumutsa ife munjira imeneyi. 

Lero, koma chokwiitsa n’chakuti Akristu ambiri sadziwa Uthenga Wabwino wa Mulungu wa ubatizo ndi mwazi wa Yesu omwe anatipatsa ife ochimwa mwa chisomo Chake, choonadi cha kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Chimaswa mtima wanga kuona anthu ambiri akukhulupilira mu ziphunzitso za Chikristu, kuchita Chikristu monga chipembedzo ndi kukakamira pa ziphunzitso za chikhalidwe chake ndipo motero kukhala mbuli pa kubadwa mwatsopano. Pali Akristu ambiri mu Korea komanso dziko lonse amene amanena kuti amakhulupilira mwa Yesu. Chikristu pa chokha chili ndi mbiri yaitali kuchokera pafupi fupi dzaka 2000, ndipo patha dzaka 500 kuchokera pa nthawi yomwe kukonzanso kunakazikitsidwa. Koma kupatula izi, pali Akristu ambiri amene ndi mbuli moti sadziwa ngakhale choonadi cha kubadwa mwatsopano, chisomo chapadera cha Mulungu. Koma ndi kukhulupilira kuti Ambuye pompano adzapanga choonadi kudziwika kwa ali yense mu masiku otsiriza. 

Ochimwa angakhale munthu olungama ndi kulowa kumwamba pokha pokha ngati iye wabadwa mwatsopano kudzera mu Mau a madzi ndi Mzimu. Akristu osawerengeka amafuna kubadwa mwatsopano ndipo akuyesera kukwaniritsa ichi. Koma ali yense amene akunena kuti munthu ayenera kubadwa mwatsopano ngakhale kuti iye sadziwa kuti kubadwa mwatsopano ndi chiani ndi wothandizira chipembedzo chabodza. Ngakhale Akristu amamva nthawi zonse kuti munthu angalowe kumwamba ngati iye wabadwa mwatsopano, ambiri a iwo sadziwa kuti ndi Mau ati amene angawapangitse kubadwa mwatsopano. M’malo mwake, iwo amangoganiza kuti abadwa mwatsopano chifukwa anakhulupilira mwa Yesu mwa njira ili yonse, chifukwa anazolowera chipembedzo, kapena chifukwa akupita muzodabwitsa zosachitika. Akristu otere akukhala moyo okhulupilira malodza m’malo mwa chikhulupiliro.Dziwani ubatizo wa Yesu, chobisika cha chitetezero cha machismo


Baibulo likunena kuti chomwe chimapangitsa kuthekera kwa ali yense kubadwa mwatsopano ndi Mau osaola amene safeka (1 Petro1:23). Tiyeni tione zomwe Mtumwi Petro analemba pa za ubatizo wa Yesu apa. Choyamba, kunalembedwa mu 1 Petro3:21, “Cimenenso cifaniziro cace cikupulumutsani tsopano ndico ubatizo.” Monga Baibulo likunena apa, ubatizo wa Yesu ndi chipulumutso chathu. Akristu onse ayenera kudziwa ndi kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu, osati ubatizo wao wa mwambo. Ngati mukhulupilira ubatizo wa Yesu ngati ntchito Yake ya chipulumutso yomwe yabweretsa moyo kwa ochimwa ngati inu, ndiye kuti mudzabadwa mwatsopano ndi kupatsidwa Mzimu Woyera kupeza chipulumutso. Izi zili chonchi chifukwa pamene mudzazindikira ubatizo omwe Yesu analandira kwa Yohane Mbatizi kuti apange chitetezero cha tchimo lililonse, ndi kutenga Mauwa a chipulumutso, mudzapulumutsidwa ku machimo anu onse kamodzi kokha, ndi kukhala munthu wolungama olandira moyo wosatha kamodzi. Kukamba zimenezi mwanjira ina, ndi mwa kulandira Mau a Mulungu mu mtima mwanu ndi kukhulupilira mu choonadi ichi cha chipulumutso ndi mtima onse kuti mwapulumutsidwa ku machimo anu onse a dziko.

Akristu ambiri amangokhulupilira mwa Yesu mwa chipembedzo chabe, koma pamene abadwa mwatsopanodi, amabadwa kachiwiri mwa chikhulupiliro atatha kuzindikira choonadi. Dzina la “Yesu” likutanthauza Iye amene “dzapulumutsa anthu Ake ku machimo ao” (Mateyu 1:29). Ngati mumakhulupilira mwa Yesu ndi kumvetsetsa kolondola pa zomwe Iye anachita kwa inu, ndiye kuti machimo anu adzasowa ndipo mudzabadwa mwatsopano ngati munthu opanda tchimo, cholengedwa chatsopano. Pamene mwalkhulupilira mwa Yesu kumene, mungakhale moyo wa chipembedzo, koma mudzabadwa mwatsopano kachiwiri ngati mwazindikira m’mene Ambuye anapulumutsira ochimwa ngati inu, ndi kumvera komanso kukhulupilira ndi mtima wanu onse mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake.

Kodi ndi choonadi chotani chomwe Ambuye wapanga kuthekera kwa ife kuti tibadwenso mwatsopano? Ndi chosaposa ubatizo omwe Yesu analandira kwa Yohane Mbatizi pa dziko lino lapansi, mwazi omwe Iye anakhetsa pamtanda, komanso kuuka kwake kwa akufa. Kukhulupilira mwa Yesu ameneyu ngati Mulungu wanu komanso Mpulumutsi wanu ndi kubadwa mwatsopano. Koma choyamba tiyeni tione m’mene anthu a Israyeli ankabadwira mwatsopano.Chitetezero cha Machimo mu Chipangano Chakale: Kuika Manja ndi Kukhetsa Mwazi


Kodi ndi Uthenga otani Wabwino omwe anthu a m’Chipangano Chakale ankabadwira mwatsopano? Tiyeni tivundukule Levitiko 1 apa kuti tione mu Uthenga Wabwino owonetsedwa mu Chipangano Chakale. Ndi zofunika kwa ife kumvetsetsa m’mene anthu a m’Chipangano Chakale ankabadwira mwatsopano. Kudzera mu ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe, Buku la Levitiko likufotokoza momveka bwino za m’mene a Israyeli ankakhalilira pamodzi ndi Mulungu. Mau a ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe ya Chipangano Chakale ndi choonadi chofunika chomwe ife tiyenera kudziwa mopanda kuchotsera. Choncho ndi zofunika kwambiri kwa ife tonse kumvetsetsa ndi kukhulupilira Mauwa 

Kunalembedwa mu Levitiko1:1-3: “Ndipo Yehova anaitana Mose, nanena naye ali m’cihema cokomanako Iye, nati, Lankhula ndi ana a Israyeli, nunene nao, Ali yense mwa inu akabwera naco copereka ca kwa Yehova, muzibwera naco copereka canu cikhale ca zoweta, ca ng’ombe, kapena ca nkhosa, kapena ca mbuzi. Copereka cace cikakhala nsembe yopsereza ya ng’ombe, azibwera nayo yaimuna yopanda cirema; abwere nayo ku khomo la cihema cokomanako, kuti alandirike pamaso pa Yehova”

Ataitana Mose ku chihema, nyumba ya Mulungu, kuti akhululukire machimo a anthu a Israyeli, Mulungu anati, “Ali yense mwa inu akabwera naco copereka ca kwa Yehova, muzibwera naco copereka canu cikhale ca zoweta, ca ng’ombe, kapena ca nkhosa, kapena ca mbuzi. Copereka cace cikakhala nsembe yopsereza ya ng’ombe, azibwera nayo yaimuna yopanda cirema; abwere nayo ku khomo la cihema cokomanako, kuti alandirike pamaso pa Yehova.” Apa, nthawi zonse pamene anthu a Israyeli achita tchimo pophwanya lamulo la Mulungu, iwo ankakhululukidwa ku ku machimo awo a tsiku ndi tsiku popereka nsembe yopanda chilema kwa Mulungu. Koma, nyama zopereka nsembe kwa Mulungu sizinali nyama zilizonse, koma zinkayenera kukhala nyama zopanda chilema zosankhidwa ndi Mulungu. Ndipo pofuna kuti zilandiridwe kwa Mulungu, nyamazo zinkayerea kuperekedwa malingana ndi malamulo Ake.

Kuti nsembe ilandiridwe ndi Mulungu, inkayenera kukhala nyama yopanda chilema choyamba, chachiwiri, ochimwa ankayenera kupatsira machimo ake pa nyamayo ake poika manja ake pamutu pake; chachitatu, munthuyo ankayenera kudula khosai la nsembe ya nyamayo ndi kuchotsa mwazi wake; pomaliza, wansembe ankaika mwazi pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza ndi kuthira mwazi otsala pansi. Umu ndi m’mene anthu a Israyeli ankapezera chikhululukiro cha machimo awo onse. Ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe m’chihema inali njira yomwe chitetezero cha machimo inkachitika, njira yomwe Mulungu anabweretsera chikhululukiro cha machimo kwa anthu onse a Israyeli mwa chisomo Chake.

Mopangidwa ndi malamulo okhazikitsidwa ndi Mulungu komanso malamulo a khalidwe pa zoyenera kuchita ndi zosayenera kuchita masiku onse moyo, Lamulo lopatsidwa ndi Mulungu muli timalamulo tosachepera 613. Ngakhale Mulungu anapatsa lamuloli kwa anthu a Israyeli, komanso a Israyeli anadziwa kuti ayenera kusunga lamulo Lake, iwo ankalephera kukhala mwa Lamulo. Izi zili chonchi chifukwa mwachilengedwe, munthu anatenga tizidutswa tonse khumi ndi tiwiri ta tchimo kwa Adamu. Choncho tinganene apa kuti munthu anataya kuthekera kochita chinthu chabwino pamaso pa Mulungu. Ali yense choncho ndi olephera kuchita chilungamo. Ndi oipa kwambiri, anthu onse ndi olephera kuchita chabwita koma zoipa mwa khumbo lawo. Ali yense anakonzeredwa kubadwa ngati ochimwa ndi kufa ngati ochimwa

Koma, Mulungu anali ndi chisoni kwambiri pa anthu otere moti Iye anawapatsa ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe komwe kunapanga kuthekera kuti kwa ali yense kupulumutsidwa ku machimo ake. Iye anapatsa iwo ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe ku chihema, kuti anthu a Israyeli ndi mtundu onse wa anthu ulandire chikhululukiro cha machimo kudzera mu ndondomekoyi ya kaperekedwe ka nsembe yoperekedwa ndi Mulungu. Kudzera mu ndondomekoyi yakaperekedwe ka nsembe, Mulungu analankhula kwa ife za chikondi Chake cha chilungamo, komanso Iye anapereka lamulo la chipulumutso kwa anthu onse.

Atapereka ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe yomwe inalola anthu kulandira chikhululukiro cha machimo, Mulungu anapatsa udindo otumikira mwambo wa nsembe wa fuko wa a Levi. Mwa mitundu khumi ndi iwiri ya Israyeli yochokera kwa ana amuna khumi ndi awiri a Yakobo, Mulungu anapatsa udindo wa unsembe ku utumiki wa nsembe kwa mtundu wa Levi. Onse Mose ndi Aroni mkulu wansembe anali wochokera ku mtundu wa Levi. Choncho malembo ananena kuti ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe inkatumikiridwa ndi ansembe a mtundu wa Levi, ndipo ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembeyi ikutanthaunza Uthenga Wabwino wa kuika manja omwe unabweretsa chikululukiro cha machimo ku a Israyeli. Choncho, kumvetsetsa bwino ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe ya Chipangano Chakale yotumikiridwa ndi mtundu wa Levi pamaso pa Mulungu ndi yofunika kwa ife kuzindikira m’mene tingabadwire mwatsopano mu nthawi ino ya Chipangano Chatsopano. Ndizofunika kwambiri kwa ife kutenga mwathunthu Mau a Mulungu okhudza ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe ya kuchihema. Ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembeyi inkatengedwa yofunika ndi Mulungu m’Chipangano Chakale, ndipo ndi yolumukizidwa mosasunthika kunsembe ya Yesu Kristu m’Chipangano Chatsopano, kudzera mowe ife tonse tadalitsidwa kuti tibadwe mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. 

Ataitana Mose, munthu wa mtundu wa Levi, kuchihema chokomanako, Mulungu anasankha mbale wake Aroni monga mkulu wansembe kuti apatsire machimo onse a chaka a Israyeli pa mbuzi yamoyo. Tiyeni tibvundukule Baibulo ndi kuona zomwe Mulungu ananena kwa Mose pomwe Iye anamuitana. Kunalembedwa mu Levitiko 1:2, “Ndipo Yehova anaitana Mose, nanena naye ali m’cihema cokomanako Iye, nati, Lankhula ndi ana a Israyeli, nunene nao, Ali yense mwa inu akabwera naco copereka ca kwa Yehova, muzibwera naco copereka canu cikhale ca zoweta, ca ng’ombe, kapena ca nkhosa, kapena ca mbuzi.” Mulungu anaikiratu nyama za nsembe zomwe zinganyamule machimo a Israyeli. Iye akunena apa kuti ngati wina wa a Israyeli akufuna kukhululukidwa machimo ake, Iye ayenera kupereka nsembe yopanda chirema kwa Mulungu ya zoweta za ng’ombe kapena nkhosa. 

Monga kunalembedwa, Mulungu apa anati, “Copereka cace cikakhala nsembe yopsereza ya ng’ombe, azibwera nayo yaimuna yopanda cirema; abwere nayo ku khomo la cihema cokomanako, kuti alandirike pamaso pa Yehova.” Mu Baibulo nsembe yopsereza ikutanthauza nsembe yomwe ochimwa wapatsira machimo yake ku nyama ya nsembe ndipo inayenera kuweruzidwa m’malo mwake, m’malo mwa ochimwa kufa chifukwa cha machimo ake pamaso pa Mulungu. Nsembeyo apa inkayenera kuladiridwa pamaso pa Mulungu mopanikizika. Nanga kodi, a Israyeli ankapereka bwanji nsembe zao kwa Mulungu kuti zilandiridwe? Yankho likupezeka mu ndime yachinai.

Mulungu akuti mu ndime yachinai, “Ndipo aike dzanja lace pamutu pa nsembe yopsereza; ndipo idzalandiridwa m’malo mwace, imtetezere.” Mfundo yolimba yomwe muyenera kumvetsetsa apa ndi yakuti munthu ankayenera “kuika dzanja lake pamutu pa nsembe yopsereza.” Izi zikutanthauza kuti, kuti nsembe ili yonse ilandiridwe ndi Mulungu mopanikizika, munthu ayenera kuika manja ake pamutu pa nsembeyo. Pamene ochimwa waika manja ake pamutu pa nsembe yopsereza machimo ake ankapatsidwa pamutu pa nyama ya nsembe, ndipo choncho asanapereke nsembeyo kwa Mulungu, ochimwayo choyanmba ankayenera kupereka machimo ake pa nyama ya nsembe mwa kuika manja ake pamutu pake. Pokhapo pamene ndondomeko yachitika ndipomwe Mulungu ankalandira nsembe mopanikizika m’malo mwa imfa ya ochimwa. 

M’Chipangano Chakale, pamene anthu a Israyeli achimwa kapena alephera kukhala mwa lamulo la Mulungu, ankayenera kupereka nyama yopanda chirema monga mbuzi, mwanawankhosa, ng’ombe yaimuna kapena nkhunda ngati chopereka cha nsembe kwa Mulungu m’malo mwao. Ndipo asanapereke nsembeyo kwa Mulungu, iwo ankayenera kupatsira machimo ao mwa kuika manja ao pamutu pake. Iwo kenako akapha nsembeyo yomwe yalandira machimo ao ndi kuchotsa mwazi wake. Wansembe kenako ankatenga mwaziwo, kuika wina waiwo pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira wotsala pansi. Umu ndi m’mene Mulungu anachitira kuthekera ku anthu a Israyeli kuti alandire chikhululukiro cha machimo ao ndi kumasulidwa ku machimowo. A Israyeli ankayenera kupereka mphotho za machimo ao mwa kupereka nsembe kwa Mulungu malingana ndi lamulo Lake loperekedwa.

Kunalembedwa mu Levitiko 1:5, “pamenepo aiphe ng’ombeyo pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, abwere nao mwazi, nawaze mwaziwo pozungulira pa guwa la nsembe, lokhala pa khomo la cihema cokomanako.” Ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe yolembedwa mu malembo ndi choonadi chofunika kuti onse a ife tikhale nacho mosachotsera ndi kumvetsetsa kwathunthu m’maganizo athu. Guwa la nsembe yopsereza linali pafupi ndi khomo la chihema, ndipo ngodya zake zinayi munali nyanga. Pamene ochimwa wapereka machimo ake ku nsembe ya mwanawankhosa mwa kuika manja ake pamutu pake ndi kuchotsa mwazi wake mwa kudula khosi, wansembe kenako ankaika mwazi wa mwanawankhosa pa ngodya zinayi za guwa la nsembe yopsereza. Mu Baibulo, nyanga za guwa la nsembe yopsereza zikutanthauza Buku la chiweruzo (Yeremiya 17:1), ndipo choncho, zoona zoti mwazi wa nyama ya nsembe inkaikidwa pa nyanga zikutanthauza kuti nsembeyo yakhetsa mwazi wake m’alo mwa ochimwa kuti ipereke mphotho ya machimo ake. Choncho Mulungu anakhululukira machimo a ochimwayu powerengera nsembe ya nyamayo, kuika manja kwa ochimwa, komanso mwazi wa nyamayo oikidwa pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza. 

Kodi n’chifukwa chiani nyama ya nsembeyo inkayenera kukhetsa mwazi wake? Chifukwa chakuti mphotho ya uchimo ndi imfa. Nyama ya nsembeyo inayenera kukhetsa mwazi wake chifukwa moyo wa chili chonse uli mu mwazi wake. Baibulo likuta mu Ahebri 9, “wopanda kukhetsa mwazi kulibe kumasuka.” Ndi chifikwa chake lamulo la Mulungu lofuna imfa ngati mphotho ya uchimo inkakumana ndi imfa ya nyama ya nsembe. Mwazi umenewu ukanakhetsedwa ndi ochimwa mwini, koma nyama ya nsembe inkaphedwa m’malo mwake, ndipo choncho wansembe ankaika mwazi wa nyama pa nyanga zinayi za guwa la nsembe yopsereza. Nyangazi zikutanthauza Buku la Ntchito kapena Buku la Chiweruzo lomwe linakambidwa mu Chibvumbulutso 20:11-15 m’Chipangano Chatsopano. Mwanjira ina, kuika mwazi wa nsembe pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza ndi chimodzi modzi kuwaza mwazi wake wa munthu pa mabuku a chiweruzo pomwe ntchito zake zonse za uchimo zinalembedwa. Zoona zoti mwazi wa nyama unali kuikidwa pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza ukuchitira umboni kuti ochimwa wapanga chitetezero cha machimo ake kudzera mu kuika manja ake komanso mwazi wa nyama yake ya nsembe. 

Tchimo la ali yense lochimwira Mulungu linalembedwa m’malo awiri. Limodzi ndi pa mtima pa munthu, ndipo lina ndi Buku la chiweruzo pamaso pa Mulungu. Baibulo limanena kuti tchimo lili lonse lopangidwa ndi ali yense limalembedwa m’malo awiri amenewa, mu mtima mwa munthu komanso mu Buku la chiweruzo pamaso pa Mulungu.

Kunalembedwa mu Yeremaya 17:1, “Cimo la Yuda lalembedwa ndi peni lacitsulo, ndi nsonga ya diamondi; lalembedwa pa colembapo ca m’mtima mwao, ndi pa nyanga za maguwa a nsembe anu.” Penapake mu Levitiko 17:11, Baibulo linalembanso, “Pakuti moyo wa nyama ukhala m’mwazi.” Mwazi ndi moyo wa munthu, ndipo ndi mwazi omwe umabweretsa chikhululukiro cha machimo. Ichi ndi chifukwa chake mwazi wa nyama ya nsembe unkaikidwa pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza. Kuonetsa kuti nyama inasenza chiweruzo cha uchimo m’malo mwa ochimwa (Ahebri 9:22). 

Kunalembedwa mu Levitiko 1:6-9: “Ndipo asende nsembe yopsereza, ndi kuikadzula ziwalo zace. Ndipo ana a Aroni asonkhe moto pa guwa la nsembe, ndi kukonza nkhuni pamotopo; ndi ana a Aroni, nsembewo, akonze ziwalozo, mutu, ndi mafuta pa nkhuni ziri pa moto wa pa guwa la nsembe; koma atsuke ndi madzi matumbo ace ndi miyendo yace; ndi wansembe, atenthe zonsezi pa guwa la nsembe, zikhale nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya pfungo lokoma la kwa Yehova.”

Monga kunaonetsedwa, wansembe ankadula nyama ya nsembe muzidutswa ndi kuitentha pa guwa la nsembe yopsereza kupereka kwa Mulungu ndipo nsembeyi imatchedwa kuti nsembe yopsereza kapena nsembe yamoto. Nsembe yopsereza apa ikutanthauza kuti pamene tachimwa pamaso pa Mulungu, tiyenera kuphedwa monga nsembe, kukhetsa mwazi wathu kamba ka machimo athu, kuponyedwa ku moto wa gahena, ndi kulandira chilango cha moto chifukwa cha machimo athu. Nsembe yopserezayi inali nsembe yomwe Mulungu anaperekera chiweruzo chake cholungama cha uchimo. Kudzera mu nsembe yopsereza ya nyama ya nsembe-ndiye kuti, kudzera mukuika manja a ochimwa pa nyama ya nsembe, mwazi wake ndi imfa, komanso nsembe yake monga nsembe yopsereza-Mulumgu anakwaniritsa lamulo Lake la chilungamo komanso lamulo Lake la chikondi. 

Chifukwa Mulungu ndi Mulungu wa chilungamo, Iye anayenera kupatsira machimo a Israyeli ku nyama ya nsembe ndi kuweruza nyamayo m’malo mwao poitentha ndi moto, ndipo chifukwa Mulungu anakonda a Israyeli Iye anaweruza machimo ao onse kudzera mu nsembe yopsereza m’malo moweruza a Israyeli. Ndipo mu nthawi ya Chipangano Chatsopano, chifukwa Ambuye wathu atikonda ife, Iye anayenera kubatizidwa m’malo mwathu, kukhetsa mwazi Wake ndi kufa pamtanda m’malo mwathu, ndipo motero akhala operekedwa m’malo mwathu. Chipulumutso chimenechi ku uchimo chomwe chinakwaniritsidwa ndi Yesu kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi chinali okhulupilira Ake onse ku machimo ao onse a dziko kamodzi kokha. Chitetezero Cha Machimo Cha M’Chipangano Chakale Cha Machimo a Tsiku Ndi Tsiku a Israyeli


Kunalembedwa mu Levitiko 4:27-31: “Ndipo akacimwa wina wa anthu a m’dziko, osati dala, pa cina ca zinthu ziri zonse aziletsa Yehova, naparamula; akamdziwitsa kucimwa kwace adacimwako, azidza naco copereka cace mbuzi yaikazi, yopanda cirema, cifukwa ca kucimwa kwace adakucita. Aike dzanja lace pamutu pa nsembe yaucimo, naiphe nsembe yaucimo pamalo pa nsembe yopsereza. Ndipo wansembe atengeko mwazi ndi cala cace, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wace wonse patsinde pa guwa la nsembe. Nachotse mafuta ace onse, monga umo amacotsera mafuta pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo awatenthe pa guwa la nsembe akhale pfungo lokoma la kwa Yehova; ndi wansembe amcitire comtetezera, ndipo adzakhululukidwa.” 

Monga mbeu ya Adamu, anthu a Israyeli ndi onse a ife tinabadwa mu dziko lino monga milu ya machimo kuchokera kuchiyambi. Choncho mtima wa munthu ndi odzadza ndi mitundu yonse ya machimo. Munthu ndi odzala ndi tchimo lili lonse, kuchokera ku maganizo oipa kufikira ku chilakolako, kupha, kudzikuza, kuba ndi kunama. M’Chilpanagano Chakale kuti anthu otere akhululukidwe ku machimo ao a tsiku ndi tsiku, ankayenera kupereka nyama ya nsembe yopanda chilema kwa Mulungu choyamba; kenako ankayenera kupereka machimo ao pa nyama kamodzi kokha mwa kuika manja ao pamutu pake pamene wansembe ankawayang’anira pa guwa la nsembe yopsereza; ndipo iwo ankayenera kupha nyamayo ndipo kenako ankapereka mwazi wake kwa wansembe. Wansembe kenako ankatumikira mwambo wa nsembe wotsalawo ndi kupereka nyamayo kwa Mulungu, ndipo zotsatira za anthu amenewa a Israyeli ankakhululukidwa ku machimo ao a tsiku ndi tsiku ndi kubwerera kunyumba opanda tchimo.

Lamulo linapangidwa ndi malamulo a Mulungu onena zoyenera kuchita ndi zosayenera kuchita kwa ali yense, koma kukanakhala kuti panalibe lamulo, kulibe akanazindikira machimo ake ngakahale atawachita iwo. Ichi ndi chifukwa chake Mulungu anatipatsa ife lamulo, kuti tidziwe machimo athu (Aroma 3:20). Kudzera mwa lamuloli la Mulungu, choncho, tiyenera choyamba kuzindikira kuti tchimo ndi chiani. Lamulo lolembedwa la Mulungu limanena zoyenera kuchita ndi zosayenera monga anakhazikitsira Mulungu, ndipo ndi pamene timadziwona tokha pa lamuloli kuti timazindikira ku machimo athu. Machimo anu sayesedwa pa chikumbumtima chanu; koma, ndi pamene mwaziona nokha pa lamulo la Mulungu kuti mwakhala ozindikira machimo anu.

Ngakhale Mulungu akufuna kufufuta machimo a munthu ali yense, Iye sangafufute machimo kwa munthu amene akuganiza kuti alibe tchimo. Choncho, kuti tirandire chikhululukiro cha machimo, munthu choyamba ayenera kuzindikira kuti ndi ochimwa. Pamene munthu wamba wa a Israyeli wachita tchimo, ambiri a iwo sankachimwira dala, koma ankachimwa mosadziwa myoyo yao chifukwa onse anabadwa ngati ochimwa mwachibadwidwe. Tchimo lili lonse lochitidwa chifukwa cha kufooka limatchedwa kuti zolakwa. Baibulo limanena kuti zolephera zonsezi, kaya zadala kapena zosadziwa, ndi machimo. Mwachibadwidwe ali yense ndi operewera. Anthu aku Israyeli naonso anali ofooka ichi ndi chifukwa chake ankachita machimo ndi zolakwa mosadziwa. Machimo ndi zolakwa za anthu zimasiyanitsidwa motere: zikhumbo zoipa ndi maganizo mu mtima mwa munthu zimatchedwa machimo, ndipo zochitidwa kamba ka maganizo a uchimowa zimatchedwa zolakwa (Aefeso 2:1). Ndipo zonse machimo komanso zolakwa pamodzi zimatchedwa machimo a dziko. 

M’Chipangano Chakale, machimo onse ankaperekedwa kudzera mukuika manja. Izi zinkakamba chikhulupiliro choti pamene munthu wapatsira machimo ake kunyama ya nsembe mwa kuika manja ake pamutu pake, iye safunika kufa chifukwa cha machimo ake, pakuti iye wakhala opanda tchimo. Umu ndi m’mene malamulo awiri a Mulungu-chikondi cha Mulungu komanso chiweruzo chake choyenera-zonse zinakwaniritsidwa mwa choonadi. Pamene Mulungu anapanga ife anthu, Iye anapanaga ife kuchokera kufumbi, ndipo choncho tinali fumbi chabe la anthu. Kunena kuti mwazi nyamaya nsembe unali kuthiridwa pansi (fumbi) patsinde la guwa la nsembe ndi kuika pa nyanga zake kukutanthauza kuti mphotho ya machimo inaperekedwa pamaso pa Mulungu komanso mu mitima ya a Israyeli. Izi zinali kuchitika chifukwa machimo omwe analembedwa mu mtima ayenera kutetezeredwa ndi mwazi wansembe.

Kunalembedwa, “Nachotse mafuta ace onse, monga umo amacotsera mafuta pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo awatenthe pa guwa la nsembe akhale pfungo lokoma la kwa Yehova.” Mu Baibulo, mafuta apa akutanthauza Mzimu Woyera. Choncho, kuti ife tipange chitetezero cha machimo athu, tiyenera kupereka nsembe kwa Mulungu malingana ndi zofunika zake, ndipo tiyenera kulandira chikhululukiro cha machimo mu mitima yathu molingana ndi ndondomeko yakaperekedwe kansembe ya chipulumutso chopatsidwa ndi Mulungu. 

Mulungu ananena kwa anthu a Israyeli kuti abweretse nsembe kwa Iye za anaankhosa, mbuzi ndi ng’ombe zamphongo. Nyama za nsembezi m’Chipangano Chakale zinali zopatulika zomwe zimabzikula, komanso yogawikana chiboda. ng’ombe ya mphongo mwachitsanzo, ndi nyama yomwe imabzikula. Nyama zoperekedwa kwa Mulungu zinkayenera kukhala zopanda chilema chifukwa Yesu Kristu, amene adzabadwa mwa Mzimu Woyera, amene adzakhala odzipereka m’malo mwathu. 

Anthu a Chipangano Chakale akanakhululukidwa machimo ao pamene iwo ankapatsira machimo ao ku nyama yopanda chilema monga nkhosa kapena mbuzi mwa kuika manja ao pamutu pake, ndipo wansembe ankapereka nsembe m’malo mwao. Chimodzi modzinso m’Chipangano Chatsopano, Yesu anasenza machimo onse a dziko kamodzi kokha mwa kubatizidwa ndi Yohane Mbatizi, kukhetsa mwazi Wake pamtanda, ndipo motero wapanga kuthekera kwa onse amene akhulupilira mwa Iye monga Mpulumutsi wao kuomboledwa ku machimo ao onse ndi kupeza chipulumutso. Pamene Wansembe Ankachita Chitetezero Cha Machimo Ao, a Israyeli Ankakhululukidwa Ku Machimo Ao Onse


Pamene tikuyang’ana m’Chipangano Chakale bwino bwino, tikuona kuti si ali yense amene ankakhala wansembe, koma amtundu wa Levi okha ndi amene anakonzedwa kukhala a nsembe. Wansembe ali yense amene akukhala wa Levi komanso mbeu ya Aroni mosachotsera. Ngati wina wake ochokera ku mtundu wina-mwachitsanzo wina ochokera ku mtundu wa chifumu wa Yuda-akuyesera kutenga unsembe kuti atumikire mwambo wa nsembe, iye ankatembeleredwa ndi khate kapena kuphedwa ndi Mulungu pomwepo. Pokhazikitsa malamulo a ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe, Mulungu anaikiratu kuti ansembe ayenera kukhala afuko la Aroni popanda kuchotsera.Aroni Ankatumikira Mwambo wa Nsembe wa Yom kippur (Tsiku la Chitetezero Cha Machimo)


M’Chipangano Chakale, pamene anthu wamba a Israyeli achita tchimo, iwo ankabweretsa nyama yopanda chilema ndi kupereka nsembe kwa Mulungu pamaso pa ansembe masiku onse. Monga mwa ndondomeko yoyamba ya kaperekedwe ka nsembe, iwo ankapatsira machimo ao ku nyama ya nsembe mwa kuika manja ao pamutu pake, ndipo kenako iwo ankadula khosi lake. Ansembe kenako ankaika mwazi wake panyanga za guwa la nsembe yopsereza, kuthira mwazi otsara pansi kudula nyamayo mudzidutswa, kuchotsa mafuta ake, kuika nyama ndi mafuta pa guwa ndi kuzitentha ndi moto. Anthu a Israyeli motero ankakhululukidwa machimo ao kudzera mu nsembe yauchimoyi. 

Chifukwa anthu a Israyeli ankapereka nsembe nthawi zonse pamene iwo achimwa, iwo analibe ziweto komanso nkhosa zokwanira zopangira chitetezero cha machimo ao osawerengeka. Choncho iwo anadziwa kubvuta kwake kolandira chikhululukiro cha machimo tsiku ndi tsiku, ndipo izi zinawabweza kumbuyo iwo kuopereka nsembe mokhulupirika. Iwo anayamba kulakalaka kusiya kupereka nsembe kwa Mulungu, poti posatengera kuti ndi nsembe zingati zomwe apereka, zinalibe malire m’maso mwao.

Izi ndi chimodzi modzi ku zoona zoti posatengera kuti ndi mapemphero angati akulapa omwe tapemphera mwa kuyesera kwathu kuti tikhale masiku onse monga mwa lamulo la Mulungu, mapemphero athu akulapa amakhala mwa chidule ku machimo athu. Choncho, chitetezero choonadi cha machimo chimapangidwa pokhapo ngati takhulupilira mwa lamulo lokhazikitsidwa ndi Mulungu la chipulumutso ndi mtima wathu onse. 

Posatengera kuti a Israyeli akhulupilira bwanji mwa Mulungu komanso ayesera bwanji kulemekeza lamulo lokhazikitsidwa ndi Mulungu ndi machitidwe ao, mphamvu zao sizinali zokwanira kwa iwo kukhala mwa lamulo. Mwanjira ina, sakanakwanitsa koma kuchimwa tsiku ndi tsiku posatengera kuti ayesera bwanji osachita tchimo. Choncho pachifukwa ichi, Mulungu anakhazikitsa njira mu ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe ya anthu a Israyeli kuti alandire chikhululukiro cha machimo onse a chaka chonse kamodzi kokha (Levitiko 16:17-22). 

Kunalembwdwa mu Levitiko 16:29, “Ndipo lizikhala kwa inu lemba losatha.” Lemba apa likutanthauza lamulo la Mulungu, ndipo izi zinafotokozedwa mwatsatanetsatane mu Levitiko 16:29-31: “Ndipo lizikhala kwa inu lemba losatha; mwezi wacisanu ndi ciwiri, tsiku lakhumi la mweziwo, muzidzicepetsa, osagwira nchito konse, kapena wa m’dziko, kapena mlendo wakukhala pakati panu; popeza tsikuli adzacitira inu cotetezera, kukuyeretsani; adzakuyeretsani, kukucotserani; zoipa zanu zonse pamaso pa Yehova. Likhala kwa inu sabata lakupulumula, kuti mudzicepetse; ndilo lemba losatha.” Anthu a Israyeli mpumulo mu mitima yao patsiku la khumi la mwezi wa chisanu ndi chiwiri, pamene mkulu wansembe ankapereka nsembe ya chaka m’malo mwao ndipo motero kupanga chitetezero ku machimo onse opezeka m’mitima yao a chaka chonse. Ndi pamene kenako a Israyeli ankapeza mpumulo m’mitima yao.

Levitiko 16:6 akunena kuti, “Ndipo Aroni abwere nayo ng’ombe ya nsembe ya uchimo, ndiyo yace yace, nacite codzitetezera iye yekha, ndi mbumba yace.” Patsiku la khumi la mwezi wa chisanu ndi chiwiri, monga mkulu wansembe mu nthawi ya Chipangano Chakale, Aroni poyamba ankayenera kupereka ng’ombe ngati nsembe ya uchimo ya iye yekha, ndipo monga nsembe zina, iye ankayenera kuika manja ake pa ng’ombe ndi kuipereka ngati nsembe yopsereza kwa Mulungu. Ndipo motero kupereka ng’ombe kwa iye yekha ndi mbumba yake, Aroni mkulu wansembe kenako ankapereka nsembe ya tsiku la chitetezero cha machimo m’malo mwa onse a Israyeli. Pa nthawiyo, a nsembe wamba sankalowa mkati mwa chihema. Choncho, pa tsiku la khumi la mwezi wa chisanu ndi chiwiri, Aroni choyamba ankapereka nsembe ya iye yekha ndi mbumba yake, ndipo kenako iye ankapereka nsembe ina m’malo mwa anthu onse a Israyeli kuti akhululukire machimo ao a chaka chonse.

Kunalembedwa, mu Levitiko 16:7-10: “Ndipo atenge mbuzi ziwirizo naziimike pamaso pa Yehova pakhomo pa cihema cokomanako. Ndipo Aroni ayese maere pa mbuzi ziwirizo; maere amodzi kwa Yehova, ndi amodzi kwa Azazeli. Ndipo Aroni abwere nayo mbuzi imene adaigwera maere a Yehova, naiyese nsembe yauchimo. Koma mbuzi imene adaigwera maere a Azazeli, aiike yamoyo pamaso pa Yehova, kuti acite nayo cotetezera, kuitumiza kucipululu ikhale ya Azazeli.” Monga taonera apa, mbuzi ziwiri zinkatengedwa pa tsiku la khumi la mwezi wa chisanu ndi chiwiri. Pa nthawiyo, akapeza chikululukiro cha machimo ake ndi mbumba yake, Aroni mkulu wansembe “ankachita maere pa mbuzi ziwiri,” imodzi yomwe inali ya Ambuye, ndi ina ya mbuzi yamoyo. 

Mu Baibulo, Mau oti “mbuzi yamoyo” akutanthauza “kumasulidwa.” Izi zikutanthauza kuti Mulungu anamasula nyama ya nsembe kwa anthu onse a Israyeli. Mbuzi imodzi inkaperekedwa kwa Ambuye choyamba, ndipo nyama ya nsembeyi inkayenera kuti mkulu wansembe aike manja ake pamutu pake mu chihema m’malo mwa anthu onse a Israyeli ndipo motero kupatsira machimo ao apachaka. Atatha kuika manja ake pamutu pa mbuzi, mkulu wansembe ankachotsa mwazi wake. Kutenga mwaziwo kupita nao m’malo oyeretsetsa, ndi kuwaza kasanu ndi kawiri pampando wachifudo mkati mwamalo oyeretsetsa, motero kupeza chikhululukiro cha machimo onse a chaka a anthu a Israyeli pamaso pa Mulungu. M’malo moika anthu a Israyeli ku imfa, Mulungu analola Aroni mkulu wansembe kupatsira machimo ao a chaka ku mbuzi yoyamba ndi kuilola kuti inyamule chiweruzo chomwe anthu a Israyeli ankayenera kunyamula, motero kupulumutsa iwo kudzera mu nsembeyi.

Kuti a Israyeli alandire chitetezero cha machimo, kunali koyenera kuti kukhale nyama ziwiri za nsembe komanso mitundu iwiri ya nsembe zoperekedwa ndi mkulu wansembe. Ndipo nsembe ili yonse inkayenera kuperekedwa malingana ndi ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe yokhazikitsidwa ndi Mulungu. Kunsembe zonse, nyama ili yonse ya nsembe inkayenera kukhala nyama yopanda chilema molingana ndi lamulo la Mulungu, koma pa nsembe ya tsiku la chitetezero cha machimo, kuonjezerapo mkulu wansembe ankayenera kupatsira machimo a Israyeli pa nyama mwa kuika manja ake pamutu pake mosalephera, kupha nyamayo ndi kuwaza mwazi wake kasanu ndi kawiri chakuno ndi uko pa Mpando Wachifundo. Umu ndi m’mene mbuzi imodzi mwa ziwirizo inkaperekedwa kwa Mulungu. Atatha kuika manja ake pamutu pa mbuzi ndi kupatsila machimo onse a chaka a Israyeli, mkulu wansembe ankapha mbuzi ndi kupereka mwazi wake komanso nyama kwa Mulungu, monga kwafotokozedwa mu Levitiko 16:18-19, “Ndipo aturukire guwa la nsembe lokhala pamaso pa Yehova ndi kulicitira cotetezera; natengeko mwazi wa ng’ombeyo, ndi mwazi wa mbuziyo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira. Ndipo awazepo mwazi wina ndi cara cace kasanu ndi katatu; ndi kuliyeretsa ndi kulipatula kulichotsera zodetsa za ana a Israyeli.”

Popanda nsembeyi yoperekedwa ndi mkulu wansembe, anthu a Israyeli sakanatha kulandira chikhululukiro cha machimo kwa muyaya, koma zikomo ku ndondomeko ya nsembe komanso mkulu wansembe okhazikitsidwa ndi Mulungu, iwo analandira chikhululukiro cha machimo ao onse a chaka kamodzi kokha. Ndondomeko yakaperekedwe ka nsembeyo inali chipulumutso cholungama cha Mulungu komanso njira yomwe Mulungu anapulumutsira a Israyeli.

Mwakusankhidwa mu unsembe monga mkulu wansembe, Aroni ankatumikira chitetezero cha machimo cha anthu ake komanso Mulungu. Aroni anali ndi udindo opereka nsembe pa tsiku la chitetezero cha machimo la khumi la mwezi wachisanu ndi chiwiri, ndipo pokwaniritsa unsembe pamaso pa Mulungu, iye ankafufuta machimo a chaka chonse a Israyeli ndi kuwatsuka iwo. Pamene anthu a Israyeli aona machimo ao akuperekedwa pa mbuzi kudzera mukuika manja a muthu umodzi, Aroni mkulu wansembe monga oimilira wao, iwo anali ndi chitsimikizo kuti machimo ao a chaka akhululukidwa. Kwa anthu a Chipangano Chakale, chipulumutso chomwe chabweretsa chitetezero cha machimo kwa anthu onse a Israyeli inali nsembe yomwe inkaperekedwa m’malo mwao ndi mkulu wansembe patsiku la khumi la mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku la chitetezero cha machimo. Mbuzi Yachiwiri Inkaperekedwa Kuchitetezero Cha Machimo a Israyeli a Chaka Chonse mu Mitima Yao


Motero atapereka mbuzi imodzi mwaziwirizo kwa Mulungu, Aroni kenako ankatenga mbuzi yotsala, monga kwalembedwa mu Levitiko 16:21-22: “”Ndipo Aroni aike manja ace onse awiri pamutu pa mbuzi yamoyo, ndi kubvomereza pa iyo mphulupulu zonse za ana a Israyeli, ndi zolakwa zao zonse, monga mwa zochimwa zao zonse; naike izi pamutu pa mbuziyo ndi kuitumiza kucipululu ndi dzanja la munthu wampagiratu. Ndi mbuziyo isenze yokha mphulupulu zonsezo kunkanazo ku dziko la pa lokha; ndipo azitaya mbuziyo m’cipululu.”

Ndi anthu onse a Israyeli akuyang’ana, Aroni ankaika manja ake pamutu pa mbuzi yachiwiri ndi kuulula machimo onse a Israyeli m’malo mwao, kunena kuti, “Ambuye, anthu a Israyeli apha, achita chigololo, kuba, kusirira komanso kukangana. Agwadira mafano, kuphwanya sabata ndi kuitana dzina Lanu pachabe. Iwo achimwa machimo onsewa ndi kulephera kusunga malamulo Anu.” Machimo onse a chaka a anthu a Israyeli ankaperekedwa pa mbuzi yamoyo pa nthawiyo. Mkulu wansembe akaika manja ake pamutu pa mbuzi yamoyo, inkamasulidwa kupita kuchipululu ndi kuzungulira yokha mpaka imfa yake.

Machimo athu ayenera kutetezeredwa mu ndondomeko ziwiri. Choyamba, tiyenera kulandira chikhululukiro cha machimo kuchokera kwa Mulungu, cha chiwiri, chitetezerochi cha cha machimo athu chiyenera kupezeka mu mitima mwathu. Kuti a Israyeli alandire chitetezero cha machimo, nyama ya nsembe inkayenera kufa chifukwa cha machimo ao olembedwa mu Buku la Mulungu la chiweruzo, ndipo mwazi wake unkayenera kuikidwa pamenepo. Ichi ndi chifukwa chake Aroni ankayenera kuika mwazi wa nyama ya nsembe panyanga za guwa la nsembe yopsereza. Ndi pamene Mulungu akaona mwaziwu iye ankatsimikizira nsembe ya a Israyeli ndi chikhulupiliro chao, kunena kuti anapanga chitetezero cha machimowo pamene machimo ao anaikidwa pa nyama ya nsembe ndipo nyama inkaweruzidwa mpaka kufa m’malo mwao. M’Chipangano Chakale, Uthenga Wabwino wa kuika manja komanso wa mwazi unali Uthenga Wabwino operekedwa ndi Mulungu wa chipulumutso omwe unabweretsa chikhululukiro cha machimo. Simuyenera kuiwala kuti izi ndi chimodzi modzinso mu nthawi ya Chipangano Chatsopano. 

Mu njira imeneyi, pamene anthu a Israyeli anabvomera kuti machimo ao anaikidwa pa mbuzi yamoyo kamodzi kokha, iwo analandira chikhululukiro cha machimo ao a chaka chonse. Anthu a Chipangano Chakale amene anakhulupilira mu nsembeyi ya tsiku la chitetezero cha machimo, kuika manja, ndi mwazi wa nsembe anakhala ndi chitsimikizo cha chipulumutso kuti machimo ao akhululukidwa. Nsembe zonse za Chipangano Chakale zinali chithunzi thunzi cha Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo m’Chipangano Chatsopano, Uthenga Wabwino omwe munthu amabadwa mwatsopano.Uthenga Wabwino wa Chitetezero Cha Machimo Owonetsedwa M’Chipangano Chatsopano


Nanga, kodi Mulungu anakwaniritsa bwanji chitetezero cha machimo kwa ali yense m’Chipangano Chatsopano? 

Kunalembedwa mu Mateyu 1:21-25: “Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamucha dzina lace Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ace ku macimo ao. Ndipo zonsezi zinakhala kuti cikacitidwe conenedwa ndi Ambuye mwa mneneri, ndi kuti onani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, ndipo adzamucha dzina lace Emanueli; ndilo losandulika, Mulungu nafe. Ndipo Yosefe anauka tulo tace, nacita monga anamuuza mngelo wa Ambuye, nadzitengera yekha mkazi wace; ndipo sanamdziwa iye kufikira atabala mwana wace; namucha dzina Lace Yesu.” 

Ambuye wathu anadza pa dziko lino monga Emanueli Mulungu kupulumutsa ife ku machimo athu onse. Ichi n’chifukwa chake Iye anamutcha Yesu. Pofuna kutetezera ndi kufufuta machimo onse a mtundu wonse wa anthu olengedwa m’chifaniziro cha Mulungu, Ambuye mwini anadza pa dziko lino mu thupi la munthu monga Mpulumutsi. Ndipo atadza pa dziko lino, Ambuye wathu anakwaniritsa ntchito Yake ya chipulumutso kupulumutsa ife ku machimo athu onse.Uthenga Wabwino wa Kusinthidwa


Kunalembedwa mu Mateyu 3:13-17; “Pamenepo Yesu anacokera ku Galileya nadza ku Yordano kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye. Koma Yohane anati amkanize, nanena, Ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi? Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse ca Mulungu motero. Pamenepo anamlola Iye. Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anaturuka m’madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye; ndipo onani, mau akucokera kumiyamba, akuti Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.” Monga zaonekera apa m’Chipangano Chatsopano, pa zaka makumi atatu Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi mu mtsinje wa Yordano kuti alandire machimo a dziko, ndipo Iye motero anapulumutsa ochimwa onse a dziko ku tchimo lao lili lonse. Mwa kulandira ubatizowu kwa Yohane Mbatizi, Yesu anakwaniritsa chilungamo chonse cha Mulungu.Kodi N’chifukwa Chiani Yesu Analandira Ubatizo wa Chikhululukiro Cha Machimo mu Mtsinje wa Yordano?


Apa Baibulo, tikuona Mkulu Wansembe wa kumwamba komanso mkulu wansembe wa dziko lino wapansi abwera pamodzi, ndipo tikuonanso kuti Yesu wakwaniritsa chilungamo cha Mulungu kudzera mu ubantizo Wake ndi kupanga chitetezero cha machimo onse kwa ochimwa ali yense mu dziko. Yohane Mbatizi, munthu amene anabatiza Yesu, anali wamkulu mwa iwo wobadwa mwa akazi. Yesu mwini anachitira umboni ku zimenezi momveka bwino mu Mateyu 11:11, “Indetu ndinena kwa inu, Sanauke wakubadwa mwa akazi munthu wankuru woposa Yohane Mbatizi.” M’Chipangano Chakale, anthu a Israyeli analandira chikhululukiro cha machimo pamene ochimwa kapena mkulu wansembe ankaika manja ake pamutu pa nyama ya nsembe. Chimodzi modzinso, m’Chipangano Chatsopano, kunali pamene Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi pomwe chitetezero cha machimo onse a dziko chinachitika, ndipo chiombolochi chimalandiridwa mwa Yesu ndi chikhulupiliro. Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo omwe umalola ali yense kubadwa mwatsopano ndi Uthenga Wabwino omwe Yesu anatetezera ndi kutsuka machimo onse a dziko. Choncho, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo unakwaniritsidwa mwa Yesu kudzera mu ubatizo Wake ndi Uthenga Wabwino operekedwa ndi Mulungu omwe unapulumutsa anthu onse ku machimo onse a dziko ndi kupanga dziko lonse kukhala lopanda tchimo kudzera mu ubatizo wa Yesu Mwana wa Mulungu, Uthenga Wabwino omwe unakwaniritsa chilungamo cha Mulungu ndi kukhululukira tchimo lili lonse la mtundu wa anthu. Yesu anabatizidwa moyenera kukwaniritsa chipulumutsochi cha ochimwa onse ndi kupanga chitetezero cha machimo ao onse. 

Kodi “chilungamo chonse” chikutanthuza chiani? Zikutanthauza ubatizo omwe Yesu analandira kupanga chitetezero cha machimo onse a anthu. Iye anabatizidwa pofuna kutsuka machimo onse a ochimwa ali yense mu dziko lino Payekha mwa Iye mwini. Baibulo likunena kuti, “Pakuti m’menemo [Uthenga Wabwino] caonetsedwa cilungamo ca Mulungu cakucokera kucikhulupiriro: kuloza kucikhulupiriro: monga kwalembedwa, koma munthu wolungama adzakhala ndi moyo ndi cikhulupiriro” (Aroma 1:17). Chilungamo cha Mulungu ndi choti Mulungu Atate anatuma Mwana Wake pa dziko lino kudzapulumutsa ali yense ku machimo onse a dziko, ndipo Atate anafufuta tchimo lili lonse ndi ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Ichi ndi chilungamo cha Mulungu cha chipulumutso.

Chilungamo cha Mulungu m’Chipanagano Chatsopano chinakwaniritsidwa mwa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Kodi ndi chilunga chotani chomwe ife ochimwa timalandira kwa Mulungu? Ndi ubatizo omwe Yesu analandira kwa Yohane Mbatizi mu njira ya kuika manja. Pafupi fupi zaka 2000 zapitazo, machimo athu onse ndi machimo onse a dziko anaperekedwa pa Yesu Kristu pamene Iye anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi, ndipo ndi chifukwa cha chipulumutso cha chilungamochi, chifukwa Yesu anasenza machimo a dziko lino, kuti takhala anthu olungama ngakhale tinali ochimwa. Ndipo chipulumutso chathu ku machimo onse chomwe chimapezeka mwa kubvomera choonadichi ndi chilungamo cha chipulumutso cholandiridwa kwa Mulungu.

kunalembedwa mu Mateyu 3:15, “Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse ca Mulungu motero. Pamenepo anamlola Iye.” Pamene Yesu anabatizidwa, “ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye; ndipo onani, mau akucokera kumiyamba, akuti Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.” Mulungu Atate mwini anachitira umboni za chipulumutso, kunena apa kuti Mwana Wake wakwaniritsa chilungamo chonse mwa kubatizidwa. Iye anena kuti, “Yesu, amene anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi, ndi Mwana Wanga.” Mulungu Atate payekha ananena apa kuti Mwana Wake anabatizidwa pofuna kupulumutsa mtundu onse wa anthu ku mphotho yace yamachimo. Iye anapereka umboni motere kutsimikiza kuti zomwe wachita Yesu Mwana Wake, ntchito Yake ya chilungamo yomwe inachotsa machimo onse a dziko, sikanaperekedwa mwachabe chabe. 

Yesu ndi Mwana wa Mulungu, komanso Iye ndi Mpulumutsi Mbuye amene anapulumutsa ochimwa onse ku machimo onse a dziko. Pamene Mulungu Atate ananena kuti, “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.” Iye ankachitira umboni kuti Yesu watenga machimo onse a dziko kudzera mu ubatizo Wake mwakulemekeza chifuniro cha Atate. Mau oti ubatizo akutanthauza kutsuka, kusamutsa, kupereka pa, ndi kukwirira. Machimo athu onse anapatsidwa pa Yesu pamene Iye anabatizidwa, ndipo choncho pamene takhulupilira mu choonadichi ndi mitima yathu, tapulumutsidwa ku machimo athu onse a dziko. 

Chipangano Chakale ndi Mau a Mulungu onenera za chipulumutso chathu, ndipo chikwaniritso chake ndi ubatizo wa Yesu. Choncho Chipangano Chakale ndi Chipangano Chatsopano pamapeto pake zinafanana pamodzi. M’Chipangano Chakale, machimo a chaka a anthu a Israyeli anapatsidwa pa nyama ya nsembe pamene nsembe ya tsiku la chitetezero cha machimo inaperekedwa, ndipo chofanana chake m’Chipangano Chatsopano ndi ubatizo wa Yesu omwe analandira kwa Yohane Mbatizi (Mateyu 3:15-17). Kunali kupulumutsa anthu onse ochimwa ku machimo a dziko kuti Yesu anabatizidwa. Chifukwa cha ubatizowu wa chitetezero cha machimo omwe yesu analandira, machimo athu onse a mu mtima anaperekedwa pa Yesu, ndipo motero, ngati wina wake wabvomera choonadichi cha chipulumutso komanso chikhululukiro cha machimo, kuti machimo onse a dziko kuphatikiza tchimo la chibadwidwe komanso machimo a tsiku ndi tsiku anaperekedwa pa Yesu, ndiye kuti machimo Ake onse adzatsukidwa kuchokera pansi pa mtima wake ndipo okhulupilirayu adzapulumutsidwa kotheratu ku machimo ake mwa chikhulupiliro.

Pokha pokha mutabvomereza panokha ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pamtanda mu mtima mwanu, simungatsukidwe ku machimo a mu mtima mwanu kuli konse mu dziko lino. Kukanakhala kuti machimo anu onse anapatsidwa ndi kufufutidwa mwanjira ina yoposa ubatizo wa Yesu, ndiye kuti izi sizinakwaniritsidwe mwa Mau a Mulungu. Chipulumutso choonadi cha anthu chimapezeka pokhulupilira kuti machimo onse a dziko anaperekedwa pa Yesu kudzera mu ubatizo Wake. Nanga mudzachita chiani? Kodi mudzabvomera choonadichi, kapena mudzachikana? Awa si mau a munthu. Ndi Mau olnkhulidwa a Mulungu. Yesu anapachikidwa mpaka kufa chifukwa Iye anasenza machimo a dziko pobatizidwa; mwazi omwe Iye anakhetsa pamtanda unali zotsatira za ubatizo Wake. Ndipo kuukanso kwa akufa, Ambuye wapulumutsa okhulupilira Ake onse. Nanga kodi Yesu sanafe pamtanda chifukwa cha zotsatira cha ubatizo omwe Iye analandira?

Baibulo linalemba mu Aroma 8:3-4, “Pakuti cimene cilamulo sicinathe kucita, popeza cinafoka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana Wace wa Iye Yekha m’chifanizo ca thupi la ucimo, ndi cifukwa ca ucimo, natsutsa ucimo m’thupi; kuti coikika cace ca cilamulo cikwaniridwe mwa ife, amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa Mzimu.” Pamene panalibe osunga lamulo la Mulungu poti ali yense anali ofooka mu thupi, Yesu Mwini anasenza machimo onse a dziko pa thupi Lake kudzera mu ubatizo Wake ndi kufufuta machimo onsewo mwa kupachikidwa mpaka kufa. Chosachotsera ichi mu choonadi cha ubatizo omwe Yesu analandira kwa Yohane Mbatizi. Ndi chifukwa chake Yesu anabatizidwa kuti Iye anafa pamtanda. Nzeruyi ya Uthenga Wabwino wakale yomwe Mulungu anakonza kutipatsa ife kuchokera pa chiyambi pa dziko kuti akhululukire machimo athu onse. 

Ngati mwakhulupulira mwa mtanda okha kwa zaka zonsezi, muyenera tsopano kulandira Uthenga Wabwino wa chipulumutso choonadi, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo omwe Yesu anabweretsa kwa inu. Pokhapo ndi pamene mungakhale mwana wa Mulungu. Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo ndi Uthenga Wabwino wa ubatizo wa Yesu, mwazi Wake, imfa Yake ndi kuuka Kwake omwe Mulungu analankhula kwa ife kudzera mu madzi ndi Mzimu. Mwa kubatizidwa mu mtsinje wa Yordano, Ambuye wathu watsuka machimo onse a dziko kamodzi kokha, ndipo mwa kukhatsa mwazi Wake wa mtengo wapatali pamtanda, Iye wapulumutsa onse okhulupilira mu chipulumutso cha ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Opulumuka apeza chipulumutso chao mwa kukhulupilira m’Mauwa a choonadi mu mitima yao. Choncho, ngakhale machimo ao akutsogolo atsukidwanso ndi kufafanizidwa mwa chikhulupiliro. Ali yense amene wapulumutsidwa mwa chikhulupiliro wa omboledwa tsopano ku machimo ake onse pokhulupilira mu choonadichi cha chipulumutso cha ubatizo wa Yesu (kuika manja), mwazi Wake pamtanda (chiweruzo), imfa Yake, komanso kuuka Kwake. Nanga inu bwanji? Kodi mumakhulupiliranso mu choonadichi? Ngati mumatero, ndiye kuti mwakhalanso munthu olungama.

Tsopano, tiyeni tisinthe zida apa ndi kuunika mwatsatanetsatane zomwe zinachitika pamene Yesu anabatizidwa. Choyamba, tiyeni tibvundukule Yohane 1:29: “M’mawa mwace anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” “m’mawa mwace” omwe alembedwa apa mu Baibulo akutanthauza tsiku lotsatira utatha ubatizo wa Yesu. Yohane Mbatizi ananena kuti Yesu anali Mwanawankhosa wa Mulungu amene ananyamula machimo a dziko lapansi. Iye anachitira umboni motere chifukwa iye anapereka machimo onse a dziko pa Yesu pa mtsinje wa Yordane kudzera mu ubatizo omwe iye anampatsa Yesu dzulo lake. Mboni inganene zomwe iyo ikudziwa. Chimodzi modzinso, ndi chifukwa choti Yohane Mbatizi anabatiza Yesu payekha kuti iye akanachitira umboni wa Ambuye ndi kunena kuti, “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” izi zikupanga chidziwitso choti Yesu anasenza machimo onse a dziko kudzera mu ubatizo Wake ndi kupereka machimowo pamtanda, ndipo chosaposa ichi ndi Mau a Uthenga Wabwino wa kusinthidwa. 


         


Monga kwanenedwa, Yohane Mbatizi anafuula, “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” (Yohane 1:29) ndimeyi ikutanthauza kuti kudzera mu ubatizo Wake, Yesu anachotsa machimo onse a dziko lapansi kochokera pachiyambi pake kufika kumapeto. Machimo onse amene munachitapo kuchokera pa nthawi yomwe munabadwa mu dziko lino kuchokera m’mimba ya amayi anu kufikira tsiku lomwe munafika zaka khumi onse ali pamodzi ndi machimo a dziko. Kodi mukuzindikira tsopano Mau a choonadi kuti machimo onsewa anapatsidwanso pa Yesu pamene Iye anabatizidwa? 

Munachimwanso mu unyamata wanu. Kodi mukukhulupilira kuti machimo onsewa anaikidwanso pa Yesu kudzera mu ubatizo Wake? Nanga kodi machimo amene munachita mu zaka zanu za makumi awiri? Kodi naonso anaperekedwa pa Yesu? Inde, kumene! Nanga za machimo amene mudzachita mtsogolo? Kodi machimo amenewanso ali pamodzi ndi machimo a dziko? Iwo ali pamodzi ndi machimo a dziko. Kodi machimo amenewanso anaikidwa pa thupi la Yesu? Kumene anaperekedwa! Kodi mukukhulupilira tsopano ndi mtima wanu onse kuti tchimo lanu lili lonse linaperekedwa pa Yesu kudzera mu ubatizo Wake? Kodi mukukhulupilira kuti Yesu anasenza machimo onse a dziko kudzera mu ubatizo Wake? 

Kodi mukufuna kuti mupulumutsidwe ku machimo anu onse a dziko tsopano? Ngati mukufuna kupulumutsidwa, ndiye khulupilirani mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pamtanda ngati chipulumutso chanu ku machimo, monga Uthenga Wabwino omwe wapanga kuthekera kwa inu kubadwa mwatsopano. Ngati mwakhulupilira mu Uthenga Wabwinowu, mudzapulumutsidwa. Mudzachita chiani tsopano? Mudzakhulupilira mu Uthenga Wabwinowu wa choonadi? Ichi ndi chipulumutso cha kusinthidwa chobvomerezeka mu ufumu wa kumwamba. Ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake muli Uthenga Wabwino oyamba wa kusinthidwa, ndipo Uthenga Wabwinowu ndi mphatso ya chipulumutso yomwe Mulungu anapereka kwa ochimwa onse kuti abadwe mwatsopano.

Chikhulupiliro chokhulupilira mu chipulumutso cha kusinthidwa komwe Ambuye anakwaniritsa kudzera mu ubatizo omwe Iye analandira komanso mwazi wa mtengo wapatali omwe Iye anakhetsa pamtanda, ndi kuyang’ana pa chikondi cha Mulungu cha chipulumutso ndi kulandira icho mu mtima-ichi ndi chikhulupiliro choonadi, ndipo ndi chomwe chimapanga kuthekera kwa ali yense kubadwadi mwatsopano. Madzi ndi mwazi wa Yesu ndi zomwe zimapanga Mau a kusinthidwa. Mwabadwa mwatsopano ngati mwalandira Mauwa a choonadi olembedwa mu Baibulo.Chipembedzo Motsutsana ndi Chikhulupiliro


Chikristu monga chipembedzo chabe zonse zili mwakupanga Yesu wao ndi kukhulupilira mu chipulumutso malingana ndi zofuna za munthu komanso maganizo. Motsutsana, chikhulupiliro cha Chikristu choonadi chomwe chimabweretsa chipulumutso kuchokera ku machimo ndi kukhulupilira chabe mu chipulumutso cha Mulungu kuptula maganizo a munthu, kukhulupilira kudalira mu zomwe Mulungu wachita kukwaniritsa lonjezo Lake la chipulumutso. Mwanjira ina, zikufunika ife kukhulupilira kuti monga m’mene Mulungu analonjezera kupulumutsa ife m’Chipangano Chakale ndi ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe m’Chipangano Chatsopano, Yesu indedi anasenza machimo a dziko lapansi mwakubatizidwa ndi kupanga ife opanda tchimo mwa kukhetsa mwazi Wake. Ndi mwa kukhulupilira nzeru ya Umulunguyi yakale ya Uthenga Wabwino kuti munthu amapulumutsidwa.

Popnda ubatizo wa Yesu palibe kupatsira machimo, ndipo popanda kukhetsa mwazi Wake, palibe chikhululukiro cha machimonso. Machimo athu onse anaperekedwa kotheratu pa Yesu ndi kutsukidwa kudzera mu ubatizo Wake, ndipo Yesu ananyamula machimo onsewa kupita nawo pamtanda ndi kukhetsa mwazi Wake wamtengo wapatali kuti apange chitetezero cha machimowo. Choncho, ndimwakubvomera Mau a nzeru, Mau a ubatizo ndi mwazi wa Ambuye, kuti timapulumutsidwa ku machimo onse a dziko. Pofuna kukhala ndi chikhulupiliro choonadi, tiyenera kukhulupilira mu chilungamo ndi chipulumutso choonadi cha Mulungu, chomwe Yesu anasenza machimo athu onse pamene Iye anabatizidwa ndi kutsuka machimowo kotheratu pamene Iye anaweruzidwa kwathunthu pamtanda m’malo mwathu. Mulungu anakonda anthu onse kwambiri kotero kuti pofuna kupulumutsa ali yense ku uchimo, Mulungu Mwini anadza pa dziko lino lapansi mu thupi la munthu, anabatizidwa kusenza machimo onse a anthu, ndipo anakhetsa mwazi Wake pamtanda kulipila mphotho ya machimo. Choncho, munapulumutsidwa mongokhulupilira mu Mau a Uthenga Wabwinowu wa kusinthidwa, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo omwe Yesu anapanga kwa inu. Ambuye anakwaniritsa Uthenga Wabwinowu mwa ngwiro kuombola ochimwa onse ku machimo ao ndi kuchiweruzo, ndipo ndi mwakulandira Uthenga Wabwinowu kuti mungapulumutsidwe ku machimo anu onse ndi kuzemba chilango chanu.

Chipulumutso chimapezeka pamene inu mwakhulupilira mu Uthenga Wabwino wa kusinthidwa opatsidwa ndi Ambuye mothokoza, kuulula kwa Iye, “Ambuye, ndikukhulupilira mu Uthenga Wabwinowu. Ngakhale ndilibe kali konse kabwino, ndikukhulupilira mu ubatizo omwe munalandira kusenza machimo a dziko, imfa Yanu, ndi kuuka Kwanu.” Motere, kulandira ndi kukhulupilira mu Uthenga Wabwino wakale wa Mulungu wa kusinthidwa ndi nzomwe chikhulupiliro cha Chikristu choonadi chikunena. 

Ndi mwachikhulupiliro kuti mwabadwa mwatsopano, monga Baibulo limanena, “Comweco cikhulupiliro cidza ndi mbiri, ndi mbiri idza mwa Mau a Kristu.” (Aroma 10:17). Baibulo limanenanso kuti, “Ndipo mudzazindikira coonadi, ndipo coonadi cidzakunasulani” (Yohane 8:32). Choncho, muyenera kudziwa choonadi cha madzi ndi mwazi Wa Yesu, ndipo muyenera kukhulupilira mu umboni wa madzi, mwazi ndi Mzimu omwe ukuchitita umboni kuti Yesu wakhala Mpulumutsi wanu wa choonadi. (1 Yohane 5:5-8).

Yesu anati, “ndipo coonadi cidzakunasulani” (Yohane 8:32). Kodi mwapezanso ufulu ku machimo anu onse molingana ndi Mau amenewo a madzi ndi mwazi, pokhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mtanda Wake? Kodi inu ndi ine tikuchita moyo wa chipembedzo, kapena tikukhala moyo wa chikhulupiliro? Ambuye akusakasaka iwo amene ali ndi chikhulupiliro mu ubatizo Wake ndi mwazi, Uthenga Wabwino omwe wapanga kuthekera kwa ali yense kubadwa mwatsopano. 

Ngati muli m’Kristu oonadi amene mumakhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo omwe Yesu wakupatsani kuti mubadwe mwatsopano, ndiye kuti mtima wanu uyenera kukhala ulibe tchimo konse. Komabe, ngati mukungokhala moyo wanu wa chipembezo, ndiye kuti ndinu ochimwa umene mtima udakali ochimwa. Ichi ndi chifukwa simukhulupilira ndi mtima wanu onse mu chipulumutso choonadi cha ubatizo ndi mwazi wa Yesu, Uthenga Wabwino wa chikhululukiro cha machimo omwe umalola ali yense kubadwanso mwatsopano. Ngati, kupatula Uthenga Wabwinowu, mukuyesera kupanga chitetezero cha machimo anu ndi kuchotsa machimowo mwa mapemphero a kulapa ku nthawi ndi nthawi, ndiye kuti mukukhala moyo wanu wa chipembedzo. Anthu otere sangapulumutsidwe ku machimo ao. Mapemphero anu a kulapa sangasinthanitse Uthenga Wabwino wa chipulumutso, Uthenga Wabwino wa kusinthidwa omwe unafufuta machimo onse a moyo wanu onse ndi kupanga chitetezero cha machimowo kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Yesu anafufuta machimo onse a dziko, kuphatikiza ngakhale machimo onse amtsogolo a okhulupilira ake, ndipo ndi pamene mwakhulupilira mu Uthenga Wabwinowu wa chitetezero cha machimo kuti mungapulumutsidwe. Kubwerezanso, palibe mapemphero a kulapa omwe amaperekedwa usana ndi usiku ndi Akristu a lero omwe angasinthanitse Uthenga Wabwino wa Yesu wa kusinthidwa, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo. Mukristu ali yense ayenera choncho kukhulupilira tsopano mu Uthenga Wabwinowu wa chitetezero cha machimo ndi kusinthidwa komwe Yesu anapereka.

Timalephera kulapa machimo athu kotheratu. Mtundu wa kulapa kwabodzaku sikubweretsa ali yense kwa Mulungu m’malo mwake, kumangobweretsa chitonthozo mwa kanthawi mu mtima mwa munthu. Pamene mwatembenuka mwa bodza, mumakana chifuniro cha Mulungu ndipo mumakamba Mau okha opanda kanthu. Mulungu safuna kutembenuka kotere. Kodi kutembenuka koona ndi kotani nanga? Ndi kubwerera kwa Mulungu. Ndi kubwerera ku Mau a chipulumutso kudzera mwa Yesu amene anapulumutsa ochimwa onse, ndi kukhulupilira mu Mau awa a choonadi monga m’mene alili. Chikhulupiliro chomwe tapulumutsidwa ndi kuchotseredwa machimo athu ndi chikhulupiliro choikidwa mu ubatizo wa Yesu, mwazi Wake, komanso kuuka Kwake kwa akufa, ndipo ndi mwakukhulupilira Uthenga Wabwinowu komwe kwatipatsa moyo osatha. Tinapulumutsidwa pokhulupilira mu Mau a Uthenga Wabwino ndi mitima yathu. Uwu ndi Uthenga Wabwino wa nzeru omwe umalola okhulupilira ali yense kubadwa mwatsopano kudzera mu chitetezero cha machimo. Ichi ndi choonadi chokhazikika cha ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, ndipo ndi Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu omwe munthu amabadwa mwatsopano pokhulupilira mwa Kristu ndi mtima onse. 

Pamene Ambuye wathu ananena kuti munthu ayenera kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu, Iye ankakamba za Uthenga Wabwino wa choonadi, kutipempha ife tibadwe mwatsopano mwa kukhulupilira mu Mau a ubatizo Wake ndi mwazi. Ndi mwakukhulupilira mu Mau a Yesu kuti tingathe kuona ufumu wa Mulungu Atate ndi kulowa mu ufumuwu. Onse a ife tiyenera kukhulupilira mu Mau a Yesu. Mau ali wonse operekedwa ndi Mulungu a chikhululukiro cha machimo olankhulidwa kwaife za ubatizo wa Yesu, mwazi Wake pamtanda, komanso imfa Yake ndi kuuka Kwake ndi Mau a kusinthidwa, ndipo ndi mwakukhulupilira mu Mauwa kuti tabadwa mwatsopano.

Nanga inu bwanji? Kodi mumakhulupilira mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, Uthenga Wabwino wa kusinthidwa? Ndi chifukwa chakuti timakhulupilira mu ubatizo wa Yesu Kristu ndi mwazi Wake pamtanda pomwe tinapulumutsidwa ku machimo onse a dziko komanso machimo athu a tsiku ndi tsiku. Kukhala ndi chikhulupiliro chotere ndi kukhulupilira mu Uthenga Wabwino wa kusinthidwa. Mwakubatizidwa, Yesu watsuka kotheratu machimo onse a ochimwa a dziko lino. Kodi inu simuyeneranso kupulumutsidwa ku machimo anu onse mwakukhulupilira mu Uthenga Wabwino wa ubatizo ndi mwazi wa Yesu omwe umalola inu kubadwa mwatsopano? 

Ambuye akunena mu ndime yamalembo atsiku la lero, “Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu” (Yohane 3:5). Ali yense amene ali ndi umboni oonadi wa Mau ukwaniritsidwa ndi Yesu-ndiye kuti, ali yense amene ali ndi Mau a ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake omwe umalola ali yense kubadwa mwatsopano-ndi munthu amene wabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Mulungu Mwini akuchitira umboni kuti chikhulupiliro cha anthu otere chimawerengedwa chilungamo mwa Iye. Monga Baibulo limanena mu 1 Yohane 5:3-10, iwo amene abadwa mwatsopano mwa chikhulupiliro ali ndi Mau a Mulungu komanso umboni Wake wa madzi, mwazi, ndi Mzimu m’mitima yao. Ngati mumakhulupiliradi mwa Yesu ndi kukhala moyo wa chikhulupiliro, ndiye kuti simuyenera kukhulupilira mu Uthenga wabodza omwe mulibe chitetezero cha machimo; m’malo mwake, muyenera kukhulupilira mu Uthenga Wabwino wa choonadi.

M’Chipangano Chakale, Mulungu anatsuka kotheratu khate la mkulu wa asilikali Namani pamene iye anamiza thupi lake mu mtsinje wa Yordano kasanu ndi kawiri (2 Mafumu 5). Chimodzi modzinso monga okhulupilira a Yesu, tiyenera kukhulupilira kuti Ambuye wabweretsa chipulumutso kwa ife ndi kupanga chitetezero cha machimo onse a dziko, ndipo motero tapeza chipulumutsochi ndi kubadwa mwatsopano mwa kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pamtanda.

Sindife amene takonda Ambuye poyamba, koma ndi Ambuye amene anakonda poyamba, ndipo choncho mungapulumutsidwenso ku machimo onse a dziko kusangalala moyo osatha mwakukhulupilira mu Uthenga Wabwino wa kusinthidwa, Uthenga Wabwino omwe Mulungu anachotsera machimo anu onse. Tiyeni tsopano tonse tikhulupilire mu Uthenga Wabwinowu wa kusinthidwa ndi kubadwa mwatsopano. Mulungu akudalitseni nonse!