Sermons

【3-15】 Mwanawankhosa wa Mulungu Amene Achotsa Tchimo Lache La dziko Lapansi!<Yohane 1:29>

M’mawa mwace anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!Kodi chinachitika ndi chiyani pamene Yesu ankafuna kubatizidwa? Kunalembedwa mu uthenga wabwino wa Mateyu 3:15, “Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse ca Mulungu motero. Pamenepo anamlola Iye.” Kodi Yesu anachotsa machimo onse adziko lapansi pamene Iye analandira ubatizo? Ndichofunika kuti tikhale ndi kumvetsetsa bwino za ‘zifukwa zimene’ Yesu anabatizidwira. Pokhapo ndi pomwe chikhulupiliro chathu chingazikike mu Mau a Mulungu, ndipo kulandira chikhululukiro cha machimo chomwe chidzatsuka chikumbumtima ndi mtima wathu.

Yesu anachotsa ngakhale machimo akutsogolo a mbumba yathu pamene Iye analandira ubatizo, koma anthu amene akunyalanyaza kukhulupilira choonadichi cha m’Baibulo ngakhale amakhulupilira mwa Iye sangapulumuke koma kukhala ochimwa m’maso mwa Mulungu. Choncho ife amene tikhulupilira mwa Yesu tiyenera kukhala kumvetsetsa kwenikweni pa chifukwa chimene Yesu analandilira ubatizo ndiponso zomwe zinachitika panthawi yomwe ankalandira ubatizo.

Kunalembedwa mu Mateyu 3:13, “Pamenepo Yesu anacokera ku Galileya nadza ku Yordano kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye.” Panthawi imeneyi mbumba yonse ya Aroni yomwe inali ya mtundu wa Levi, inkayenera kukwanitsa zaka makumi atatu isanasankhidwe monga akulu a nsembe. Ndipo a Levi ankakwanitsa kugwira ntchito zamasiku onse za kupereka nsembe m’malo opatulika kwa anthu pamene afika zaka makumi awiri ndi zisanu. Koma kuti akhale mkulu wansembe, munthu ayenera kukwanitsa zaka makumi atatu, omwe anali malamulo a Mulungu kwa iwo. Monga chonchi ambuye wathu anayenera kulandira ubatizo pamene Iye anakwanitsa zaka makumi atatu.

Pokhapo pamene Yesu analandira ubatizo wake zinaonetsa chidziwitso choyamba cha ntchito ya chipulumutso yomwe inapulumutsa anthu onse ku machimo awo. Pasanachitike ubatizowu Yesu ankachita ntchito  wamba ndi kukhala monga m’mene munthu aliyense amakhalira kusamala banja Lake. Koma pamene anafika zaka makumi atatu, Yesu anayamba utumiki wa opulumutsa Athu. Timatcha kuti “moyo wapoyera wa Yesu,” ndiko kunena kuti, moyo opulumutsa anthu onse.

Choncho funso, kodi chinthu choyambilira chomwe Yesu anachita kupulumutsa anthu chinali chiani? Yankho ndi lakuti; Iye analandira ubatizo wake kuchokera kwa kapolo osankhidwa otchedwa Yohane Mbatizi. Ichi chinali chiyambi cha uthenga wabwino wa chitetezero cha machimo a anthu onse.

Yesu anayenera kulandira ubatizo kwa Yohane Mbatizi panthawiyo. Choncho funso lina; kodi Yohane Mbatizi ndi ndani? Iye ndi kapolo osankhidwa wa Mulungu amene anadza miyezi isanu ndi umodzi Yesu asanabwere. Mulungu anatumiza Yohane Mbatizi miyezi isanu ndi umodzi patsogolo pa Yesu. Ndichofunika kuti tidziwe zimenezi, chifukwa zikutiuza ife kuti Mulungu anapanga zinthu ziwiri zimenezi zazikulu kuti zichitike padziko lino pofuna kupulumutsa inu ndi ine komanso anthu onse ku machimo awo. Agogo abala mwana komanso namwali wabala mwana zinali zosaposa ntchito yapadera ya Mulungu kuti apulumutse ife kumachimo athu. Ambuye wathu anakonza chipulumutso chathu motere. Iye anakonza motere pofuna kupulumutsa anthu onse ku machimo awo.  

Munthu osankhidwayu otchedwa Yohane Mbatizi amene anabatiza Yesu anakwanitsanso zaka makumi atatu zakubadwa. Choncho Mau akutiuza ife za munthu ameneyu “sanauke wakubadwa mwa akazi munthu wamkulu oposa Yohane Mbatizi” (Mateyu 11:11). Yesu ankatiuza ife kuti, “mwa iwo akubadwa mwa akazi, Yohane Mbatizi ndiye wamkulu. Ndidzatuma Eliya amene ndinalonjeza kutumiza, ndipo iye ndiye Yohane Mbatizi. Yohane Mbatizi ndi wamkulu mwa iwo obadwa mwa mkazi ali yense.” Mulungu anakhazikitsa Yohaneyu ‘oimilira wa anthu’ monga mkulu wansembe omaliza wa Chipangano Chakale komanso wa dziko lino.

M’Chipangano Chakale pamene mkulu wansembe anali ndi mwana wamwamuna, iye ankalandira mphamvu ya udindo ya mkulu wansembe pamene wafika dzaka makumi atatu za kubadwa. Polandira mphamvuyi ya udindo wa ‘mkulu wansembe’ kunali chimodzi modzi ngati kudzodza mbusa masiku ano. Atate ankayenera kudzodza ndi mafuta komanso kuika manja ake pamutu pa mwana wake, ndipo pamene atate ake achotsa manja ao iwo ankapatsira udindo ndi mphamvu pa mwana wake amene kenako ankapereka nsembe pa tsiku la chitetezero cha machimo a chaka chonse m’malo opatulika monga ‘oimilira wa anthu ake onse.’

Mu nthawi ya Chipangano Chakale, mkulu wansembe ankayenera kupereka nsembe ya tsiku la chitetezero pa tsiku la khumi la mwezi wa chisanu ndi chiwiri. Izi zinali molingana ndi ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe yomwe Mulungu anakhazikitsa kwa iwo, ndipo ichi chinali chithunzi thunzi cha ‘chinthu cheni cheni’ chili mkudza m’Chipangano Chatsopano (Ahebri 10:1). Choncho funso lotsatira; kodi Mulungu anatuma ndani? Choyamba, Mulungu anatuma Yohane Mbatizi. Yohane Mbatizi ndi wamkulu mwa iwo amene akubadwa mwa azimayi ndipo iye anakwaniritsa ntchito ya mkulu wansembe pamene iye anafika dzaka makumi atatu zakubadwa; iye anabadwa ngati wa fuko la Aroni mkulu wansembe.

 Funso lina lotsatira ndi “kodi Yesu ndindani?” Yesu ndi Mpulumutsi wa anthu. Popeza Chipangano Chakale chinakhazikitsa zaka zimenezi zoyenera kwa mkulu wansembe, choncho chimodzi modzi zaka zimenezi ndi zoyenera m’Chipangano Chatsopano kugwiritsidwa ntchito; ndipo popeza Chipangano Chakale chikhazikitsa ntchito ya mkulu wansembe mwa kupereka machimo a Israyeli kamodzi kokha poika manja patsiku la chitetezero cha machimo, choncho Mulungu anatuma Yohane Mbatizi pa dziko lino ndi kumupatsa iye kuti agwire ntchito ya unsembeyi; ndipo Yesu nayenso anayenera kudza pa dziko lino monga nsembe ya Mwanawankhosa, amene anayenera kuperekedwa kwa Mulungu monga oimilira wa anthu onse.

Choncho Yesu analandira ubatizo kwa Yohane Mbatizi. Ndazindkira kuti chiyambi changa ndichokulilako pang’ono. Koma gwirizanani ndi ine pamene ndiri ndi zambiri zolankhula pa nkhani imeneyi. Kodi Yohane Mbatizi ndindani kweni kweni? Kodi iye ndi oimililadi wa mtundu wa anthu, kapena ai? Baibulo limatiuza ife kuti iye indedi ndi oimilira wa anthu onse.

Tiyeni tiwerenge mau kuchokera mu Uthenga Wabwino wa Mateyu 11:10-12 pamodzi. “Uyu ndiye amene kunalembedwa za iye, kuti, onani Ine nditumiza mthenga wanga pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu m’tsogolo mwanu. Indetu ndinene kwa inu, Sanauke wakubadwa mwa akazi munthu wankuru woposa Yohane Mbatizi; koma iye amene ali wocepa mu Ufumu wa Kumwamba ankulira iye. Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa kumwamba uli wokangamizidwa, ndipo okangamirawo aukwatula ndi mphamvu.” Ndipo mu ndime 13, “Pakuti aneneri onse ndi cilamulo cinanenera kufikira pa Yohane.” Tsopano, tiyeni tilongosole zimemezi. Ambuye wathu anati kulibe munthu anauka wamkulu oposa Yohane Mbatizi mwa iwo akubadwa mwa mzimayi. Kodi mau awa “Sanauke wakubadwa mwa akazi munthu wankuru woposa Yohane Mbatizi” akutanthauza chiani kweni kweni? Akutanthauza kuti Yohane Mbatizi ndiye oimililadi wa mtundu onse wa anthu.

Ngati Aroni anali ‘woimilira wa a Israyeli onse’ m’Chipangano Chakale, nanga kodi oimilira wa anthu onse m’Chipangano Chakale ndi Chatsopano ndindani? Kodi ndindani wamkulu wakubadwa mwa akazi? Iye ndi osaposa Yohane Mbatizi amene anabatiza Yesu. Yohane Mbatizi amene anabatiza Yesu ndi oimilira wa anthu onse. Abale ndi alongo, kodi mukumvetsetsa moona amene ‘ali oimilira wa mtundu onse wa anthu’ tsopano?

Pulezidenti wa dziko lathu wapita m’maiko a ku Europu tsopano, sichonch? Kodi mukuganiza kuti iye akuchita chiani m’maiko amenewu? Kodi iye sakukulisa ubale wa ukazembe ndi kusaina mgwirizano wa zamalonda ndi zina zotero monga ‘oimilira wa dziko lathu?’ kodi inunso mukuchita ntchito zimenezi? Kapena mukungonera zomwe iye akuchita? Koma kodi iye akuchitira ndani zimenezi? Pulezidenti amalankhula m’maiko amenewa ndi kusaina mgwirizano obwereza ndi kugwira ntchito yonse yofunika. Koma ndiuzeni pamene asaina mgwirizanowu; kodi inunso simunasaine?

Kodi dzina la mgwirizano wa zachuma wa maiko otukuka makumi atatu mu dziko lino ndi chiani? Kodi si mwachidule monga OECD? Ngati pulezidenti wapiti kwinakwake ndikusaina kuti alowe mu OECD, ndiye kuti inu ndi ine tasainanso kuti tilowe mu bungweli. Mu dziko lino ndikukhulupilira kuti inunso, ndi oimilira wa chigawo chili chonse. Momwemonso pali kuimilira kwa ife anthu komwe kukupezeka.

Nanga ndi ndani oimilira  wa anthu onse? Iye ndi osaposa Yohane Mbatizi. Mulungu anasankha iye monga oimilira. Dzina la ‘Yohane’ likuonekera m’malembo ambiri, koma ‘Yohane ameneyu’ amene anabatiza Yesu ndiye osaposa oimilira anthu onse. Mudzayamba kukhala ndi kumvetsetsa kwakukulu pa malembo ‘ndikumvetsetsa kumeneku.’

Pamene Yesu ankayesera kulandira ubatizo kwa Yohane Mbatizi, iye anafuna kuti amkanize ndi kunena kuti, “ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi?” Tsopano kodi Yesu ndi ndani? Mulungu anakazikitsa Yesu monga Mkulu wansembe wa ufumu wakumwamba. Mwanjira ina, Mulungu Atate wakhazikitsa Mwana Wake ngati Mkulu wansembe wa ufumu wakumwamba-ndipo kwa okhawo amene alandira chikhululukiro cha machimo ndipo choncho alibe tchimo chifukwa cha Yesu, adzalowa ndikukhala m’malo osangalatsawa.

Ngati Yesu ndi Mkulu wansembe wa ufumu wakumwamba, tsopano funso ndi lakuti “kodi ndi ndani mkulu wansembe pa dziko lino lapansi?” Iye ndi Yohane Mbatizi. Akulu akulu ansembewa anakumana mu mtsinje wa Yordano. Iwo ankayenera kukumana, si choncho?

Mkulu wansembe wa Chipangano Chakale ankabweretsa mbuzi ziwiri ndikuzipereka nsembe pa tsiku la chitetezero cha machimo. Choncho chifukwa Mulungu analonjeza kuti adzachotsa machimo athu onse motere, Yesu sakanangonena kuti, “Yohane ndidzafufuta machimo onse a dziko. Ndidzachita monga mwakufuna kwanga. Choncho, osadandaula ndi zimenezi. Ndidzachita zimenezi ndekha.” Mulungu anayenera kuchita ntchito imeneyi chimodzi modzi monga Iye analonjezera.

Choncho, Yesu monga mkulu wansembe wa Ufumu wa Kumwamba anadza pa dziko lino mu thupi la munthu, ndipo pamene Iye anakwanitsa dzaka makumi atatu zakubadwa, Iye ananyamula machimo onse a dziko pa thupi Lake pofuna kukhala nsembe ya Mwanawankhosa, ndipo Iye anakhetsa mwazi Wake chifukwa cha machimowo pa thupi Lake, choncho chimodzi modzi nsembe zinkadulidwa khosi ndikukhetsa mwazi wake ndi kufa m’Chipangano Chakale. Yesu anadza pa dziko lino kudzachita ntchito imeneyi. Mulungu anatuma Yohane Mbatizi pa dziko lino monga oimilira wa anthu onse kudzagwira ntchito yopatsira machimo onse a dziko pa Yesu.

Choncho tikuona mkulu wansembe wa dziko lino akukumana ndi Mkulu wansembe wa ufumu wa kumwamba. Pamene iwo anakumana, kodi wamkulu anali ndani? Kodi wamkulu pakati pa Mkulu wansembe wa Ufumu wa Kumwamba ndi mkulu wansembe wa dziko lino? Mkulu wansembe wa Ufumu wa Kumwamba ndiye wamkulu. Madzi a mtsinje wa Yordano ankayenda pamodzi bwino bwino monga ankachitira nthawi zonse. Yohane Mbatizi anali pakati pa mtsinjewu ‘mpaka mchiuno’ pamene iye ankabatiza anthu. Kenako patsikulo, Yesu anadza kwa iye. Yesu anadza kwa Yohane Mbatizi ndi kumuuza iye kuti ambatize Iye. koma Yohane anaona mwachangu kuti Yesu uyu ndi Mwana wa Mulungu, Mkulu Wansembe weni weni wa Ufumu wa Kumwamba. Kenako iye anaganiza, “ndinu oimilira wa Ufumu wa Kumwamba ngakhale ndili oimilira chabe wa dziko lino.” Ndi chifukwa chake Yohane Mbatizi ananena kwa Yesu, “ndiyenera kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi? Kodi mungabatizidwe bwanji ndi ine?”

Ntchito ya unsembe ya Yohane Mbatizi inali kupereka machimo onse a dziko pa Yesu, koma kodi chikhazikitso cha nsembe yoyamba ndindani? Nsembe ya mwanawankhosa m’Chipangano Chakale inali Yesu Kristu ameneyu. Yesu Kristu anauza Yohane Mbatizi kuti ambatize Iye pofuna kutenga machimo onse a dziko lapansi pa Iye yekha, koma Yohane Mbatizi ananena mu mayankhulidwe a umunthu, “Ndinu wamkulu oposa ine. Kodi ndingakubatizeni bwanji, pamene ine ndiyenera kubatizidwa ndi Inu?”

Koma tiyenera kuyang’ana mosamara pa zomwe Ambuye ananena apa. Kunalembedwa, “Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse ca Mulungu motero. Pamenepo anamlola Iye.” (Mateyu 3:15). Yesu anamula Yohane ‘Balola zimenezi.’ Tsopano tiyeni tione Mau amenewa ochokera mu mutu wachitatu mu ndime 15 zomwe akutiuza. Yesu anauza Yohane Mbatizi, “Balola tsopano pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero,” Mau awa “motero” apa akutanthauza kuti Yesu anatetezera machimo onse a anthu polandira ubatizo kwa Yohane Mbatizi ndi kupanga onse amene akulupilira mu ubatizo wa Yesu kukhala opanda tchimo.

Abale ndi alongo, kodi n’chifukwa chiani Yesu analandira ‘ubatizo’? kodi tanthauzo la ubatizo ndi chiani? Kodi cholinga chakulandira ubatizo chinali chiani?  Yesu analandira ubatizo pofuna kupulumutsa mtundu onse wa anthu ku machimo ao, pofuna kutsuka machimowa ndikufufuta kotheratu. Yesu analadira ubatizowu. Iye anati, “Balola tsopano pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse.” “chilungamo chonse” chikutanthauza ntchito zonse za chilungamo. Nanga kodi ntchito za chilungamozi ndi chiani? Zikukamba chabe za ubatizo omwe Yesu analandira, ndipo zilibe ntchito ndi ubatizo wathu. 

Mau akuti chilungamo mu Chitchaina ndi ‘yi’ (義), omwe ndi malembo awiri, ‘wo’     (我, I) komanso ‘yang’ (羊, mwanawankhosa). Kodi izi sizosangalatsa? Pamene ndinadalila pa Mwanawankhosa wa Mulungu, ndinakhala munthu olungama mwa chipulumutso cha mwanawankhosayu. Monga mukuona apa ndi chimodzi modzi ndi njira yomwe mkulu wansembe ankagwiritsa ntchito kuika manja ake pamutu pa mbuzi kapena nkhosa m’Chipangano cha nthawi yakale.  Pamene mkulu wa nsembe waika manja onse pamutu pa nsembe, iye ankati, “Mulungu nda chimwa machimo awa. Ndipo a Israyelinso achimwa machimo amenewa. A Israyeli apha, aba komanso achita zilakolako.” “kuika manjaku” kunali kupereka machimo onse pa nsembe.

Tsopano, kodi ubatizo ndi chiani? Ubatizo omwe Yesu analandira kwa Yohane Mbatizi omwe ndi chimodzi modzi ndi kuika manja pamutu pa Yesu kunali kuchotsa machimo a anthu mwakusamutsa machimowo kuika pa thupi la Yesu. “Chilungamo chonse” ndi ntchito ya Yesu yomwe Iye anabwerera ndi kuchita mu dziko lino mwakutenga machimo athu onse ndikupanga ife anthu, opanda uchimo. Yesu ananena kwa Yohane Mbatizi, “pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero,” ndipo Iye analandira ubatizo Wake. Kulandira ubatizo kwa Yesu kukutanthauza kuti machimo athu onse anaperekedwa pa Iye. Machimo onse a anthu anaperekedwa pa Yesu pamene Iye analandira ubatizo.

Kunalembedwa, “pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero. Pamenepo anamlola Iye.” Makamaka ndabweretsa mau oyamba mu chiGreek kuti ndifotokoze zomwe akunena mu chilankhulo choyambilira, ngakhale kuti sindimadziwa bwino chiGreek. Ndidzawerenga mu chiGreek, mumvetsere mwatcheru. Kwalembedwa, “Αποκριθεις δε ο ιησους ειπεν προς αυτον αφες αρτι ουτως γαρ πρεπον εστιν ημιν πληρωσαι πασαν δικαιοσυνην τοτε αφιησιν αυτον.” Tiyenera kumvetsetsa ku mau amene adulidwa nzere pansi pake, “ουτως” komanso “πασαν δικαιοσυνην.” Liwu la mu chiGreek “ουτως” (hutos) kutanthauza ‘mnjira iyi yokha,’ ‘moyenera kwambiri,’ kapena ‘palibe njira ina yoposa iyi.’ Ndipo mau oti “πασαν δικαιοσυνην” (pasan dik-ah-yos-oo’-nayn) kutanthauza moyenera popanda bvuto lili lonse. Choncho, ndimeyi ikutanthauza kuti Yesu anachotsa machimo onse a anthu mosasinthika pa Iye yekha mnjira yoyenera kudzera mu ubatizo Wake omwe Iye analandira kwa Yohana Mbatizi. 

Mauwa akunena kuti machitidwe a Yesu kulandira ubatizo kwa Yohane Mbatizi komanso Yohane Mbatizi kubatiza Yesu motere kunakwaniritsa ntchito yosefukira ya kufufuta machimo onse a dziko; kufufuta machimo onse ku mitima ya munthu ali yense. Ndipo Yesu anatanthauza, “pakuti ‘kuyenera’ (πρεπο; prepo) kukwaniritsa ntchito imeneyi mosefukira polandira ubatizo kuti apange anthu onse, ochimwa onse, mbumba yonse ya Adamu kukhala opanda uchimo kotheratu; ndipo pofuna kukwaniritsa ntchitoyi yochotsa machimo onsewa moyenera ndi mwa ngwiro popanda vuto lili lonse Ndalandira ubatizo kwa iwe ndipo iwe wandibatiza Ine. Choncho ndi koyenera ndi kokwanira kukwaniritsa chilungamo chonse komanso utumuki wa chipulumutso chomwe chapanga anthu onse kukhala opanda uchimo.” Ili ndiye tanthauzo la mau oyambilira.

Kodi Yesu analandira ubatizo kwa Yohane Mbatizi? Kodi iye analandira kapena iye sanalandire ubatizo? Iye analandiradi ubatizo. Kodi iyi ndi nkhani yabodza chabe monga m’mene anthu akuganizira? Kodi izi zikutanthauza kuti Iye analandira ubatizo popanda cholinga chapadera? Ai, si choncho.

Mtsinje wa Yordano umadziwika kuti mtsinje wa imfa. Kuli nyimbo yomwe imanena kuti, “♬ muzokoma pang’ono ndi pang’ono tidzakumana pa gombe lokoma. ♪” Tiyenera kuoloka mtsinje wa Yordano ndi kukumana ndi Yesu kumwamba komanso gahena zimaonekera pokhapo pamene taoloka mtsinje wa imfawu. Ndi mwachilengedwe kuti munthu ali yense abadwe mu dziko lino kamodzi ndi kufanso kamodzi, ndipo pambuyo pake chiweruzo. Choncho tiyenera kufa mu mtsinje wa Yordano kamodzi, pamene Yesu anakwaniritsa chilungamo chonse mwakunyamula machimo athu onse ndi kufa pamtanda wa nkhaza m’malo mwathu pofuna kupanga ife amene takhulupilira kulowa Ufumu popanda kulephera iye anakwaniritsa zimenezi mwathunthu. Iye anati, “pakuti kuyenera if kukwanirirtsa chilungamo chonse motero.” Mu chiGreek, “kukwaniritsa” ndi “πληρωσαι” (prerosai), izi zikutanthauza kupanga mosefukira, kudzadzitsa mpaka pamwamba popanda kulephera. Zikutanthauza kuti kupanga china chake kusefukira.

Monga mwanawankhosa wa nsembe wa Chipangano Chakale ankalandira machimo onse a chaka a Israyeli pa tsiku la khumi la mwezi wachisanu ndi chiwiri ndi kutsuka machimo onse amenewa kotheratu popanda tchimo lotsara; Yesu chimodzi modzinso anadza pa dziko lino ndi kukwaniritsa ntchito yopulumutsa anthu onse kumachimo awo mokwanira: Iye wapulumutsa ife mtundu onse wa anthu ku mwa kulandira ubatizo “kamodzi kokha” kuti achotse machimo onse a anthu mwa Iye yekha ndi nyamula machimowa kupita nao pamtanda ndi kukhetsa mwazi Wake wapadera pamtanda paja. Pofuna kuti Yesu akwaniritse izi, Iye anayenera kulandira ubatizo ponena kuti, “Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero.” 

Yesu indedi analandira ubatizo kwa Yohane Mbatizi. Kodi ubatizo wa Yesu ukukamba chiani kweni kweni? Ukuchotsa machimo onse a ife anthu onse. Yesu anadza pa dziko lino pofuna kuchotsa machimo onse a anthu ‘monga Mwanawankhosa wa Mulungu,’ monga chikhazikitso cheni cheni cha ndondomeko yakaperekedwe ka nsembe m’Chipangano Chakale. Ndi chifukwa chake Yesu analandira ubatizo Wake. Kunena kuti Yesu analandira ubatizo kukutanthauza kuti mphotho ya machimo onse a anthu inaperekedwa mwathunthu.

Monga a Israyeli ankalandira chikhululukiro cha machimo ochuluka onse a chaka pa tsiku la chitetezero pamene mkulu wansembe ankaika manja ake onse pa mbuzi yamoyo; chimodzi modzinso Yesu, amene ndi Alefa komanso Omega, anadza pa dziko lino ndi kupanga anthu onse kupanga kukhala alibe uchimo kotheratu potenga machimo ao onse ndi kuika pa Iye yekha mwa kulandira ubatizo, machimo akuyamba kwa anthu mpaka kutha kwa dziko. 

Izi zikutanthauza kuti chilungamo chonse cha chipulumutso cha Mulungu chinakwaniritsidwa pamene Yesu anapereka mphotho ya machimo a ochimwa onse mwa kulandira ubatizo ndi kukhetsa mwazi Wake pamtanda. Ichi ndiye chilungamo cha Mulungu. Ichi ndiye chilungamo cha Yesu. Ngakhale chilungamo chathu chili monga zobvala zonyansa, chilungamo cha Yesu ndi chowala kwamuyaya. Kunalembedwa mu Yohane 8:32, “”Ndipo mudzazindikira coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani.” Yesu ndiye choonadi. Yesu ndiye Mpulumutsi oonadi. Iye ndi njira ya choonadi. Iye ndi moyo weni weni. Yesu analandira machimo athu onse pa Iye yekha polandira ubatizo.Kodi m’malembo akunena pati zimenezi?


Athu amafunsa; kodi m’malembo akunena pati kuti machimo a dziko  anaperekedwa pa Yesu pamene Iye analandira ubatizo Wake. Ubatizo wa Yesu ndi kuika manja kwa Chipangano Chakale ziri ndi tanthauzo lofanana. Chipangano Chakale ndi chithunzi thunzi cha lonjezo, ndipo Chipangano Chatsopano chinakwaniritsa zonse. Kodi ndi zofanana kapena ndi zosiyana? Ndi zofanana.

Tsopano pamene tiwerenga Buku la Yoswa mutu wachitatu, tikhonza kuona kuti pamene Mose anafa, Yoswa anakhala mtsogoleri wao watsopano, ndipo iye anatsogolera a Israyeli m’nzinda wa Kanani. Bvuto loyamba lomwe iwo anakumana nalo pofuna kulowa mu nzindawu linali kuoloka Nyanja ya Yordano moyenera. Mulungu anauza Yoswa pa zakaolokedwe ka mtsinje wa Yordano. Mulungu analonjeza, “ansembe onyamla Likasa ayenera kuika mapazi ao mu mtsinje wa Yordano. Kenako madzi amene akuyenda adzaleka pomwepo ndi kuundana ngati khoma la madzi, pansi padzakhala poumilatu, chifukwa madzi amene akuyenda kuthila ku Nyanja ya kufa adzadulidwa kotheratu. Kenako mudzalowa mu nzinda wa Kanani poyenda pansi pouma pakati pa mtsinje.”

Choncho Yoswa ananena kwa ansembe, “nyamalani Likasa lanu pa mapewa anu ndi kulowa mu mtsinje wa Yordano patsogolo pa anthu onse. Pamene iwo anaponda m’madzi, madzi analeka kuyenda ndipo anaundana pa malo amodzi ndi kungoimilira pafupi ndi nzinda wa Adamu. Kodi Likasali likutanthauza chiani? Kunena kuti Likasa linaimilira mu mtsinje wa Yordano, akukamba kwa ife za ubatizo wa Yesu, Mau amene anasandulika thupi ndi kukhala pakati pathu.”

Yesu ndi Mulungu wa Mau (Yohane 1:1). Yesu anadza pa dziko lino mu nthawi ya Chipangano Chatsopano, ndikuthetsa machimo onse a dziko lino mwa kutenga machimo onse a anthu pa thupi Lake kudzera mukulandira ubatizo kwa mkulu wansembe otsiriza wa dziko lapansi wotchedwa Yohane Mbatizi. Iye “motero” anakwaniritsa lonjezo lomwe Iye anapanga m’Chipangano Chakale. Ili ndiye tanthauzo la zochitika mu mtsinje wa Yordano.

Kodi Ambuye wathu wafufuta bwanji machimo lero? Iye wafufuta machimo athu ndi Mau Ake. Iye ‘wawerengera chilungamo’ kwa iwo amene akhulupilira m’Mau Ake monga Abrahamu anachitira. Ndi chipulumutso chomwe chimatetezera machimo kwa iwo akhulupilira m’Mau Ake.

Yesu analandira Ubatizo. Kwalembedwa, “Balola tsopano pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero. Pamenepo anamlola Iye.” Abale ndi alongo, kodi Yesu analandira ubatizo kapena sanalandire? Iye indedi analandira ubatizo. Kodi zikutanthauza chiani kuti Yesu analandira ubatizo? Zikutanthauza kuti Iye anachotsa machimo athu onse pa Iye yekha. Kodi ndizolondola, kapena ai? Molingana ndi Baibulo izi ndizolondola. Nanga kodi izi zikutanthauza kuti Ambuye sanatenge pa Iye Yekha machimo amene tidzachita mtsogolo? Machimo onse, tchimo lili lonse linaphatikizidwa m’mau oti “chilungamo chonse,” zomwe zikutanthauza kuti Ambuye wathu anachotsa machimo onse a dziko lino pa Iye Yekha. Kwalembedwa, “Pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse,” izi zikutanthauza kuti Ambuye anakwaniritsa chilungamo chonse.

Kodi inu ndi ine tinalipo pamene Yesu ankalandira ubatizo? Yesu anakwaniritsa chilungamo chonse cha anthu mu mtsinje wa Yordano pafupi fupi dzaka 2000 zapitazo. Yesu anachotsa machimo athu onse ngakhale machimo a iwo amene adzabadwa mtsogolo mokwanira ndi ubatizo Wake. Yesu anasesa machimo onse a dziko ndipo Iye anawaika pa Iye Yekha mwa ngwiro popanda kusiyapo ngakhale limodzi kumbuyo, ndipo motero wapanga mtundu onse wa anthu kukhala opanda tchimo. Kodi nanga mudakali ndi uchimo ngakhale kuti Yesu anasesa machimo onsewa ndi kuwanyamula onse pa mutu Pake? Ai, mulibe. 

Yesu wathu ndi Mbuye amene anachotsa machimo ngakhale amtsogolo. Iye anati kwa Yohane Mbatizi, “Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero.” Pamenepo Yohane Mbatizi anabatiza Yesu; izi zikutanthauza kuti ntchito yonse yotenga machimo onse a dziko inakwaniritsidwa mwa ngwiro ndi mokwanira. Motero, ntchito ya Yesu yotenga machimo onse kamodzi ndi kulandira chilango pamtanda kamodzi inakwaniritsidwa mosefukira.

Mudzalandira ‘chikhululukiro cha machimo’ ngati mwakhulupiliradi kuti Yesu anachotsa machimo anu onse a kutsogolo, kuti Yesu anachotsa ngakhale machimo a mbumba yanu yonse, kuti Yesu wathu anachotsa ngakhale machimo a mwana omaliza wa mzimayi amene adzabale pa tsiku lomaliza la dziko lino, ngakhale kuti sitidziwa nthawi idzakhala bwanji komanso dziko lidzapitilira motani. Kwalembedwa, “Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero. Pamenepo anamlola Iye.” 

Yesu indedi analandira ubatizo. Ndipo Yesu anaturuka m’madzi. Izi zikutanthauza kuti Yesu anamizidwa pansi pa madzi. Iye anabatizidwa mwa kumizidwa thupi lonse. Mau oti ‘ubatizo’ mu chiGreek ndi “βάφτισμα” (baptisma), omwe akutanthauza kuti “kumizidwa.” Ndi chifukwa chake mpingo wa Baptisti ndi mipingo ina yofanana imanena kuti a Kristu ayenera mosalephera kulandira ubatizo wa kumiza thupi lonse. Ndipo kumizidwa Kwake kukutanthauza imfa Yake pamtanda. Pamene Yesu anabatizidwa atatha kutenga machimo onse pa Iye Yekha ndi kuturuka m’madzi, miyamba inatseguka ndipo Mzimu wa Mulungu unatsika ngati nkhunda. Kenako Mulungu Atate anati, “Uyu ndiye Mwana Wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.” Izi zikutanthauza kuti Mulungu Atate anafufuta machimo onse adziko kwathunthu kudzera mwa Mwana Wake, mwa Iyeyo akondwera. Pamene Ankalunjika Pamtanda Atalandira Ubatizo Wake


Pamene Iye analandira ubatizo Wake, panatenga dzaka zitatu kuchokera pa nthawiyo kufikira pamene Iye anapachikidwa pamtanda. Iye anakhala moyo wa utumiki kwa dzaka zitatu. Uthenga Wabwino wa Yohane mutu wa chisanu ndi chitatu tikuona Yesu akukumana ndi mkazi monga chitsanzo amene anagwidwa chigololo. Afarisi ndi alembic anakokera mkaziyo kwa Yesu akumuimba mlandu. Ali yense wa iwo ananyamla mwala m’manja mwao kwinaku akuloza zala zao kunena kuti, “Yesu wakhala ukunena mobwereza za chikondi, chikondi ndi chikondi. Choncho chifukwa wanena mopitiliza za chikondi, kodi timteme mwala mkazi wa chigololoyu kapena ai? Tiuze ife zoyenera kuchita.” Yesu kenako modekha anawerama ndikuyamba kulemba pansi, “amene mwa inu ali wopanda cimo, ayambe kumponya mwala.” Ndipo pamene Iye anaweramuka atatha kulemba poyamba ndipo anati, “amene mwa inu ali wopanda cimo, ayambe kumponya mwala.”  Osati okhawo amene anali ndi miyala m’manja mwao, koma anthu onse a dziko lino amene sakhulupilira kuti Yesu analandira ubatizo ndi kufa pamtanda ndi ochimwa. Afarisi ndi Alembi sanakhulupilire mwa Yesu. Kodi zingatheke bwanji kwa munthu amene sanakhulupilire mwa Yesu molondora kukhala opanda tchimo? Iwo ankangofuna kumtema mwala chotere, koma Yesu anaboola mu mtima yankhaniyi. Iye anawauza iwo momveka bwino, “iye amene alibe tchimo mwa inu, ayambilire kumtema mwala. Inu muli ndi uchimo ndipo inunso ndinu ochimwa. Nanga tsopano kodi ochimwa angaweruze bwanji ochimwa mnzake mpaka kupha? Pamene Ambuye anawauza momveka bwino iwo kuti ali yense mwa iwo amene analibe tchimo ayambilire kuponya mwala, iwo anazindikira zimenezi, pang’ono pang’ono kutaya miyala yao ndi kuchoka pa malopo, ena ananena kuti akufunika apite kukadula nkhuni za moto, pamene ena ananena kuti akuyenera kukadyetsa ng’ombe, ndipo motere otsutsa onse amkaziyu anathawa kuyabira wamkulu kufikira wamng’ono, monga palibe chomwe chinachitika.”

Yesu anawerama kachiwiri ndi kulemba pansi, kenako anaweramuka ndi kunena kwa mkaziyu, “Inenso sindikutsutsa iwe.” Chomwe Iye ankamuuza chinali choti Iye sanganenenso kuti mkaziyu anali ndi tchimo. N’chifukwa chiani zinali choncho? Iye ananena kuti, “ndinachotsa machimo ako onse mwa thupi Langa polandira ubatizo wanga chifukwa cha ochimwa ngati iwe, chifukwa ndinadziwa kuti udzakhala ukuchimwa chotere mu dziko lino. Ndiri ndi machimo pa thupi Langa osati chifukwa chakuti ndinachita tchimo lili lonse, koma ndine obvomerezeka kutenga machimo amenewa ndi kulandira chilango choopsa kupulumutsa ochimwa ngati iwe. Ndiyenera kulandira chilango kwa Mulungu Atate.” Ndi chifukwa Ambuye wathu ananena kwa mkaziyu “mkazi, Inenso sindikutsutsa iwe.”

Ife anthu sitingakwanitse koma kuchimwa machimo mitundu khumi ndi iwiri yolembedwa mu Baibulo tsiku ndi tsiku mpaka tsiku la kutha kwathu. Kodi izi ndi zoona kapena ai? Izi ndi zoona. Kodi mukudzidalira kuti simudzachimwa kuchokera tsopano? Ai. Simungadzithandize koma kuchimwa chifukwa ndinu operewera. Palibe njira yoretsa kuti inu musachite tchimo mpaka tsiku la kufa kwanu. Ndichifukwa chake Ambuye wathu anakwaniritsa chilungamo chonse. Yesu anachotsa machimo onse popanda kulephera mwa kulandira ubatizo Wake ndi kutipanga ife opanda tchimo.

Yesu analandira ubatizo omwe unachotsa machimo onse a mtundu onse wa anthu. Ndipo pamene Iye anaturuka m’madzi, Mulungu Atate anati, “Mwana Wanga wafufuta machimo anu onse. Iye ndi Mwana Wanga ndipo mwa Iyeyu ndi kondwera. Mwana Wanga amene mwa Iyeyu ndikondwera sanachite tchimo lili lonse kuchokera pachiyambi, ndipo ngakhale Mwana Wanga ndi Mlengi wanu komanso Mulungu ndi Ambuye, Iye anakhala Mpulumutsi wanu.” Choncho Mulungu wathu Atate anakweza Yesu pamwamba mu dziko lino. Mulungu anakweza Mwana Wake mpaka pamwamba. Mulungu anapanga Iye kulandira ulemelero waukuru. Mwana wa Mulungu analemekeza chifuniro cha Mulungu mwa kuchotsa machimo onse a anthu a dziko lino, ndipo analandira ubatizo molingana ndi chifuniro Chake. Ndi chifukwa chake Mulungu Atate anati, “Uyu ndiye Mwana Wanga wokondedwa mwa Iyeyu ndikondwera.” Yesu ananyamula machimo athu onse pa Iye Yekha polandira ubatizo ndipo kudzera mu ntchito imeneyi, wapulumutsa ife kumachimo athu onse. 

Choncho pamene Yesu analandira ubatizo Wake kumwamba kunamtsegukira Iye ndipo Mulungu Atate anachitira umboni payekha ponena kuti, “Uyu ndiye Mwana Wanga wokondedwa mwa Iyeyu ndikondwera.” Okondedwa okhulupilira anzanga, kodi mukumvetsetsa chomwe izi zikunena kwa ife? Pamene Yesu ankafuna kulandira ubatizo Wake, Iye anati kwa Yohane Mbatizi, “Balola tsopano: Pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero.” Pamenepo Yohane Mbatizi anamlola Iye. Kodi mukukhulupilira kuti Yesu anachotsa machimo onse a athu kuphatikiza machimo anu onse pa Iye Yekha mwakulandira ubatizo Wake kuchokera kwa Yohane Mbatizi? Kodi mukukhulupilira kuti machimo amene anali mwa inu kuchokera pa nthawi yomwe munapezeka m’mimba mwa mayi anu komanso machimo amene munachita kuchokera pamene munabadwa kufika dzaka khumi zakubadwa, dzaka makumi awiri zakubadwa, dzaka makumi atatu, machimo onse amene mwachita kufikira tsopano, anaikidwa pa Yesu? Ngakhale simudziwa chomwe chidzachitika kwa inu mtsogolo, kodi mukukhulupilira kuti Yesu anachotsa pa Iye Yekha ngakhale machimo amene mudzachita mawa, machimo a mkucha, machimo onse amene mudzachite mpaka kufa kwanu, machimo a mbumba yanu, ndi machimo onse a anthu onse a dziko lino?“Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!”


Tiyeni tione Mau kuchokera mu Uthenga Wabwino wa Yohane mutu oyamba ndime 29. Kwalembedwa, “M’mawa mwace anaona Yesu alinkudza kwa Iye, nanena, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” Patatha tsiku la ubatizo wa Yesu ndi Yohane Mbatizi, anthu ambiri anamzungilira Yohane. Ndipo Yesu ankayenda momdutsa Yohane Mbatizi pa tsiku lotsatira utatha ubatizo Wake. Kenako Yohane Mbatizi anamuzindikira Iye ndikufuula ndi mau okweza, “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” Yohane Mbatizi anapereka machimo onse a dziko pa Yesu a dzulo lake mu mtsinje wa Yordano. Ndipo m’mawa mwace wa tsiku lotsatira utatha ubatizo wa Yesu, pamene Yesu ankayenda modutsa Yohane, Iye anachitira umboni mokweza kwa anthu kunena kuti, “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lache la dziko lapansi! Iye ananyamula machimo onse a dziko. Iye ndi Mwana wa Mulungu Mpulumutsi wathu, odzipereka kwa anthu onse. Iye ndi Mpulumutsi amene anapanga chitetezero cha machimo athu onse.”

Okondedwa okhulupilira anzanga, tiyenera kumvetsetsa kuti ‘tchimo lache la dziko’ ndi chiani. Tiyenera kumvetsetsa kuti tchimo la dziko likutanthauza chiani monga kunalembedwa m’Mau a Mulungu. Machimo a dziko ndi machimo amene timachita kuchokera pa nthawii yomwe tinapezeka m’mimba mwa mayi athu kufikira pa nthawi ya kufa kwathu; machimo amene tmachita pamene tikupuma mu dziko lino mpaka pa nthawi ya kufa kwathu. Ngakhale anthu ambiri sanaphunzire maphunziro ‘malingana ndi malembo,’ iwo akunena kuti machimo amene munthu anali nao pamene anali m’mimba mwa mayi ake ndi machimo a chibadwidwe ndipo zolakwa zomwe munthu wachita pamene iye anali wamng’ono atangobadwa kuchoka m’mimba mwa mayi ake monga kulila, kudzikodzera pali ponse, komanso zolakwitsa zomwe iye wachita pamene anali mnyamata ndi machimo ake a tsiku ndi tsiku. Iwo amayesera kugawa motere, koma tiyenera kudziwa kuti malembo sagawa tchimo motere. Chifukwa Mulungu ndi Wamkulu, Iye wanene kuti machimo onse amene mwachita kuchokera pa nthawi yomwe munapezeka m’mimba mwa mayi anu mpaka tsiku la kufa kwanu, onse ndi machimo a dziko, muyenera kumvetsetsa zimenezi. 

 Machimo a dziko amene Yesu ananyamula ndi osiyana ndi m’mene timaonera ife kuti ndi tchimo. Kuona kwathu ndi kwakung’ono. Nanga, kodi Mulungu wathu akunena chiani? Iye wanena chabe kuti, tchimo la dziko lapansi, monga kwalembedwa, “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” ngati izi ziri choncho, kodi Yesu anachotsa machimo onse, kapena ai? Iye anachotsadi machimo onse a dziko. Iye anachotsa machimo onse a dziko, kodi Iye sanatero? Ndikofunika kuti tizindikire lingaliro la Mauwa moyenera.

“Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” ndisanabadwedi mwatsopano, ndinkatanthauzira ndimeyi ndi maganizo anga motere: “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa chimo lache la dziko lapansi? ndi tchimo liti lomwe mukukamba pamene ine sindinachite machimo akutsogolo?” choncho ndinkatanthauzira monga “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo langa loyamba!” ndinkatanthauzira motere mwa ine ndekha ndi kuwerenga motere kusintha mau amalemba kuti afanane ndi m’mene ndi kumvera.

Choncho machimo anga sankafufutidwa ngakhale ndinkayesera chotani kuwafufuta. Zingakhale chimodzi modzi kwa inu, ngakhale kuti munalandira chikhululukiro cha machimo omwe inu munachita mpaka lero, mudzakhalanso ochimwa mawa pamene mwachitanso tchimo. Ndi chifukwa chake muyenera kulandira chikhululukiro cha machimo kawiri kawiri mobwereza bwereza. Nzosatheka kufufuta machimo anu onse mnjira imeneyi. Kodi tchimo la dziko ndi chiani? Kodi inu ndinu munthu wa dziko lino kapena ai? Inu ndinudi munthu wa dziko lino, ngati si choncho kodi ndinu mlendo? Ngakhale kuti kukanakhala alendo, iwo akanakhalanso anthu a dziko lino. Ndife anthu amene timakahala mu dziko lino lomwe Mulungu analenga kuchokera ku chiyambi kufikira pa mapeto.

Ngakhale atumwi analandira chipulumutso mwakukhulupilira mwa Yesu dzaka 2000 zapitazo. Abrahamu ndi Davide analandira chikhululukiro cha machimo pokhulupilira kuti Yesu adzadza ndi kufufuta machimo ao onse. Yesaya mneneri analemba, “Zooonadi Iye ananyamula zowawa zathu, ndi kusenza zisoni zathu” (Yesaya 53:4), komanso “Pakuti mwaponya m’mbuyo mwanu macimo anga onse” (Yesaya 38:17). Mulungu Atate anaponyera machimo athu onse kumbuyo kwa Mwana Wake. 

 Anthu a Chipangano Chakale ankalandira chikhululukiro cha machimo mwa chikhulupiliro, ndipo anthu a chikhulupiliro m’Chipangano Chatsopano alandiranso chikhululukiro cha machimo pokhulupilira kuti Yesu anachotsa machimo ao onse mwa Iye Yekha polandira ubatizo mu mtsinje wa Yordano ndi kusenza chilango chonse pamtanda. Tsopano dzaka pafupi fupi 1900 zatha kuchokera pomwe chinthu chachikulu chinachitika, kodi inu ndi ine timalandira chikhululukiro cha machimo pokhulupilira mwa Yesu? Kapena kodi chikhululukiro cha machimo mwa ntchito zathu? Timalandira chikhululukiro cha machimo pokhulupilira mwa Yesu mnjira yoyenera. Inu ndi ine talandiranso chikhulukiro cha machimo pokhulupilira mwa Yesu ndikulandira chipulumutso chathu kwa Yesu amene anadza mwa madzi, mwazi ndi Mzimu.

Kwalembedwa mu Uthenga Wabwino wa Yohane 3:5, “Indetu, Indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa Ufumu wa Mulungu.” “Madzi ndi Mzimu” apa zikutanthauza kuti Yesu analandira ubatizo; kuti Mzimu Woyera unasandulika munthu ndi kuchotsa machimo athu onse mwa kulandira ubatizo; Yesu analandira chilango pamtanda; ndipo Yesu amene ndi Mulungu anakhetsa madzi ndi mwazi pamtanda.

Chidziwitso cha Yesu kupulumutsa inu ndi ine kotheratu; ndi ntchito ya Yesu kunyamula machimo onse pa Iye Yekha pamene Iye analandira ubatizo, komanso imfa Yake pamtanda inali imfa yathu. Imfa Yake inali imfa yathu ndipo Iye analadira ubatizo pofuna kupulumutsa ife ku machimo athu. Yesu anadza pa dziko lino monga Mwanawankhosa wa Mulungu amene adzachotsa machimo a dziko. Yesu anadza pa dziko lino dzaka 2000 zapitazo ndi kuchotsa machimo onse a dziko lapansi. Iye anasenza machimo onsewa ndi kulandira chilango chachikulu pamtanda.

Tiyeni tiganizire mosamara pa zanthawi yomwe Yesu anachotsa tchimo la dziko lapansi. Ngati machimo amene mumachita ali pamodzi ndi tchimo la dziko lapansi, kodi Yesu anachotsa machimo onse a dziko lapansi, omwe akuphatikiza machimo anu onse, kodi Iye anatero? Iye indedi anachotsa machimo onse a dziko lapansi… Kodi Yesu anachotsa machimo a zidzukulu zanu? Iye indedi anachotsa machimo onsewa. Kodi Yesu anachotsa machimo a chidzukuru chathu, chidzukuru chake, komanso mbumba yake yonse machimo onse a anthu obadwa mu dziko lino mpaka kutha kwa dziko lino, machimo onse a mitundu yonse ya dziko, kapena Iye sanachotse? Iye indedi anachotsa machimo onsewa. Nanga kodi muli ndi tchimo kapena mulibe? Mulibenso tchimo tsopano. Mulungu Wakwaniritsa Chilungamo Chonse


Kwalembedwa, “Pakuti mphotho yace ya ucimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu” (Aroma 6:23). Mphotho ya uchimo ndi imfa, koma kupatula izi Yesu anachotsa machimo athu onse mwa Iye Yekha. Choncho chinthu chokhacho chinatsala kwa Iye ndi kufa pamtanda. Iye analandira chilango m’malo mwathu malingana ndi Lamulo la Mulungu lomwe likunena kuti; mphotho ya uchimo ndi imfa. Kodi Yesu anafa pamtanda, kapena ai? Iye indedi anafa pamtanda. 

Iye analila atakhomeredwa pamtanda, “kwatha” Iye asanapume mpweya Wake omaliza. Yesu anamaliza zonse. Yesu anati, “Pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero” pamene Iye ankabatizidwa-ndipo anatsimikiza zimenezi ponena kuti, “kwatha” pamtanda. Kodi pali chinachake cholephera pa chipulumutso chake chokwanira? Ai. Kodi tidzakhala ndi tchimo ngati tachitanso tchimo mtsogolo? Ai, sitidzakhalanso ndi tchimo. Kodi muyenera kuchita tchimo monga m’mene mukufunira chifukwa mulibenso tchimo? Ai simuyenera. Anthu amachita tchimo ngakhale kuti iwo amayesera osachita tchimo. Yohane Mbatizi anafuula, “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” Kodi Mwanawankhosa wa Mulunguyu anali ndani? Kodi sanali Yesu? Indedi anali Yesu, ndipo Iye anali Ambuye amene anachtsa machimo onse a dziko lonse lapansi.

Ngati izi ndi zoona kodi mwakhulupilira mwa Yesu tsopano? Kodi mukukhulupilira kuti Yesu anachotsa machimo onse a dziko ndi kutetezera machiwo? Kodi mukukhulupilira kuti machimo anu onse anaperekedwa pa Yesu pamene Iye analandira ubatizo mu mtsinje wa Yordano? Muyenera kukhulupilira moyenera mu zinthi ziwiri izi zofunika: madzi ndi mwazi. Kalata yoyamba ya Yohane pakunena momveka bwino kuti madzi, mwazi ndi Mzimu ali amodzi. Mulungu anapulumutsa ife kudzera mwa madzi, mwazi ndi Mzimu. Yesu ndi Mulungu wa Mzimu mwachiyambi. Mzimu ndi Mulungu, ndipo Mzimu unabvala thupi la munthu ndi kudza pa dziko lino ndi kulanandira ubatizo. Iye anachotsa machimo athu onse pa Iye Yekha. Ndipo Iye anakhetsa madzi ndi mwazi pamtanda. Iye analandira chilango chonse. Iye motere anapulumutsa inu ndi ine kotheratu.

Ngati tinayenera kukhulupilira mpaka tsopano popanda kudziwa momveka bwino za chipulumutso cha Yesu chokwanira, ndipo ngati tilibe chitsimikizo kuti talandila chikhululukiro cha machimo, ndiye kuti taphunzira molakwika ndipo chikhulupiliro chathu mwa Yesu ndi cholakwika. Mu Uthenga Wabwino wa Mateyu 3 ndime 15, Yesu anati pamene ankafuna kulandira ubatizo Wake, “Pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero.” Yesu anachotsa machimo athu onse pa Iye Yekha mwakubatizidwa ndipo kenako ananyamula machimowo kupita nao pamtanda. Izi ndi zoona za mu Baibulo. Machimo athu onse anaperekedwa pa Yesu. Kodi ndime ya tsiku la lero ikunena kuti machimo athu anaperekedwa pa Yesu kapena ai? Indedi ikunena kuti machimo onse anaperekedwa pa Iye. Tanthauzo la lemba loyamba likunena ndendende choncho.

Mau oti “ubatizo” akutanthauza “kukwilira, kumiza, kutsuka.” Ngati malemba akunena kuti Yesu anakwiliridwa pamene Iye anabatizidwa, ngati akunena kuti Yesu anafa chifukwa cha machimo athu onse, ngati akunena kuti Yesu analandira ubatizo pofuna kutsuka ife ku machimo athu, ngati akunena kuti Yesu analandira ubatizo chifukwa cha chimenecho, ndiye kuti tiyenera kuona lingaliro la lemba ndikumvetsetsa cholingachi chimene Yesu analandira ubatizo. Mau oti “motero” akutathauza kuti Yesu anapanga anthu onse a dziko lino kukhala alibe tchimo mwakutenga machimo onse a anthu pa Iye Yekha polandira ubatizo kwa Yohane Mbatizi, oimilira wa anthu, amene anali wamkulu oposa wonse obadwa mwa akazi. Ubatizo wa Yesu ndi chidziwitso choti Iye anachotsa machimo onse a anthu onse a dziko lino.Kodi Yesu Analindira Ubatizo Chifukwa Iye Ananyansidwa?


Kodi mukuganiza kuti Yesu analandira ubatizo chifukwa Iye analibe chochita kuti utumiki Wake udziwike kapena chifukwa Iye ankafuna kudzichepetsa Kwake? Palibe chosafunika mu ntchito zonse zomwe Yesu anachita pa dziko lino. Zonse ndi zofunika. Yesu analandira ubatizo ndi kufa pamtanda pofuna kupulumutsa inu ndi ine, komanso pofuna kuombola ife ku machimo athu onse. Kodi ndipati pomwe m’malemba Mulungu akunena kuti Yesu analandira ubatizo pongofuna kudzichepetsa kapena kuti Iye analandira ubatizo pofuna kukhala chitsanzo kwa ife?

Ngati wina afunsa chifukwa chimene Yesu analandira ubatizo mwa ‘kuika manja,’ ndiye kuti yankho langa lidzakhala; kunyamula machimo onse a dziko a thupi Lake. “motero” mu Mateyu 3:15 akutiuza ife chifukwa chimenechi. Akufotokoza chifukwa kwa ife. Akunena kuti Yesu analandira ubatizo kwa Yohane Mbatizi ndipo Yohane Mbatizi anabatiza Yesu pofuna kukwaniritsa chilungamo chonse; kunali koyenera kuti Yesu alandire ubatizo pofuna kukwaniritsa chilungamo chonse; ndipo kunali koyenera kuti Yesu afufute machimo athu onse mwa kulandira ubatizo. Kodi izi ndi zoona kapena ndi zabodza? Ndizodziwika kuti ndi zoona malingana ndi Baibulo. Ngati izo ndi zomwe Mau a Mzimu Woyera akutanthauza, ndiye kuti muyenera kukhulupilira.

Kodi ntchito yoyamba ya utumiki wa Yesu wapoyera inali chiani? Inali Iye kulandira ubatizo. Yesu analandira ubatizo kwa Yohane Mbatizi. N’chifukwa chiani Yesu analandira ubatizo? Yesu analandira ubatizo pofuna kuchotsa machimo athu onse pa Iye Yekha, pofuna kutenga machimo onse a dziko pa Iye ndi kupanga ife opanda tchimo mwakutichotsera machimo athu onse. N’chifukwa chiani Yesu anafa pamtanda Iye anafa pamtanda pofuna kulandira chilango chonse m’malo mwathu, ndipo motero kutetezera machimo athu onse. Okendedwa okhulupilira anzanga, kodi izi ndi zoona kapena ai? Mwachidziwikire izi ndi zoona. Koma chokwiitsa Akristu ambiri a masiku ano akutsutsa zimenezi, ndikufunsa choonadichi motero; kodi ndipati m’malembo pomwe akunena kuti machimo anaperekedwa pa Yesu pamene Iye analandira ubatizo. 

Kunali koyenera kuti Yesu alandire ubatizo pofuna kufufuta machimo athu onse. Kodi inu mukukhulupiliranso motere? Kodi muli ndi tchimo kapena ai? Palibe chifukwa kuti inu mukhale ndi tchimo. Palibe chifukwa kuti inu mukhale ndi tchimo ngati mukidziwa ndi kukhulupilira mwa Yesu molondola. Komabe, Akristu ambiri masiku ano amakhulupilira ndi chitsimikizo kuti analandira chikhululukiro cha machimo okha akale, ndipo akuyesera molimba kulandira chikhululukiro cha machimo ao a lero ndi akutsogolo, mwakupereka mapemphero akulapa tsiku ndi tsiku komanso kuyesera kukhala mosamala. Mwachidule, akuyesera kupeza chiyeretso mwakukhala moyo wa ntchito za bwino. Ndipo kuonjezera zimakhala zobvuta kwambiri kuyeretsedwa pamene anthu akukula. Anthu amakhala ouma mtima kwambiri komanso kupsa mtima kwao kumapitilira pamene iwo akukula.

Koma kodi chiyeretso mu dziko ndi chiani? Kodi malembo akunena kuti tidzapita kumwamba ndi machimo athu akusowa pang’ono pang’ono pamene tikuyesera kudziyeretsa? Kunalembedwa, “Pakuti m’menemo caonetsedwa cilungamo ca Mulungu cakucokera kucikhulupiriro kuloza kucikhulupiriro: monga kwalembedwa, koma munthu wolungama adzakhala ndi moyo ndi cikhulupiriro” (Aroma 1:17). Timakhala olungama mwa chikhulupiliro ndi kukhalanso mu dziko lino mwa chikhulupiliro.  Chilungamo cha Mulungu chinaonekera chokha mu Uthenga Wabwino, ndipo Yesu ndi Ambuye wa Uthenga Wabwino. Kukhulupilira mu ‘chilungamo’ ndi kukhulupilira kuti Mulungu anachotsa machimo athu onse kotheratu ndipo kuti Yesu anapanga ife opanda tchimo mwa ngwiro polandira ubatizo kuphatikiza chilango pamtanda. Kodi mumakhulupilira motere? Ngati mumakhulupilira ndiye kuti munakhala ‘olungama’ kamodzi kokha mwachikhulupiliro. 

Mtumwi Paulo akuti, “Chifukwa cace tsopano iwo akukhala mwa Kristu Yesu alibe kutsutsidwa. Pakuti cilamulo ca Mzimu wa moyo mwa Kristu Yesu candimasula ine ku Lamulo la ucimo ndi la imfa” (Aroma 8:1-2). Ndipo kwalembedwa mu Buku la Yesaya, “Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu ziri zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale ziri zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbu” (Yesaya 1:18). 

Kuyesera kulandira chikhululukiro cha machimo tsiku ndi tsiku ndi chipembedzo chabe. Takhala olungama pamene tinakhulupilira kuti Yesu analandira ubatizo kusenza machimo athu onse. Kodi izi ndi zoona kapena ai? Ngati Yesu sakanalandira ubatizo, sizikanatheka kuti ife tikhale opanda tchimo. Kodi ngongole ingaperekedwe pongonena kuti yaperekedwa popanda wina wake oipereka? Kodi Yesu ndi Mbuye ndi Mpulumutsi wa mau chabe? Yesu sanatipulumutse ife ndi mau okha. Yesu, Mulungu, indedi anabvala thupi la munthu ndikudza padziko lino. Iye anadzichepetsa Yekha. Iye anadza pa dziko lino mwa umunthu ndi kulandira ubatizo pofuna kupulumutsa mtundu onse wa anthu ku machimo ao. Iye sananene izi ndi milomo Yake chabe. Ambuye anachotsa machimo atgu onse ndi kulandira chilango pamtanda pofuna kupulutsa ife ku imfa. Yesu anapachikidwa mpaka kufa pamtanda chifukwa cha machimo a dziko. Choncho, Ambuye sanakhale Mpulumutsi wathu mwa mau chabe, koma Iye anakhaladi Mpulumutsi wathu ndi Ambuye. Yesu ndi Mpulumutsi wathu ndi Ambuye. Nkhani Ya Mtengo Wa Magetsi


Ndikufuna ndikuuzeni nkhani yosangalatsa. Kale kalero panali abale amene anali osaphunzira. Mbale wamkulu ankagwira ntchito kutali ku mnzinda wa ukulu kufuna ndalama. Pamene tsiku lolandira ndalama linafika iye anabwerela kunyumba ndi kukakumana ndi mphwake. Panatenga nthawi yaitali kuchokera pamene anyamata awa anakwera phiri lomwe linali pafupi ndi kunyumba kwao, choncho anaganiza zokwera phiri poti inali nthawin ya tchuthi. Kunalibe mitengo ya magetsi yambiri pa nthawi imene mbale wake wamkuluyo ankachoka, koma pa nthawiyo kunali mitengo ya magetsi imene inadzalidwa.

Choncho kunali zizindikiro zambiri zomwe zinaikidwa pamtengo uli onse wa magetsi zonena kuti, “chenjerani ndi moto oopsa. Onani chozimitsira moto mosamara. Chenjerani ndi moto usiku ndi usana.” Koma anyamata onsewa anali osaphunzira. Iwo ankangozindikira kuti mau akuda alembedwa pa choyera. Anyamata awa sanadziwe tanthauzo la chenjezo la zizindikirozi. 

Kunali thengo  loopsa  m’mphirimo ndipo amfumu anali pa chiopsezo chotaya ntchito yao ngati moto wabukanso. Chifukwa chakuti moto oopsa unali pali ponse mnyengo youma, iwo anaika zikwangwanizi pali ponse. Choncho chifukwa choti mbale wamkuluyu anachokera ku mnzinda waukulu atabvala chobvala chapamwamba ndi nsapato zowala, mphwakeyo anaganiza kuti mkulu wakeyo angadziwe mauwa pa zikwangwanizi popeza anachokera ku mnzinda waukulu. Choncho pamene iwo ankakwera phiriro wamng’onoyo anafunsa mkulu wakeyo, “mbale, kodi mau ali apowo akunena chiani? Kodi akunena chiani pa chikwangwani chaikidwa pamtengo wa magetsi?” “chenjerani ndi moto” chikwangwanicho chinalembedwa motero.

Koma, mkulu wakeyo anali osaphunzira ndipo sanadziwe chili chonse. Iye sanaphunzire chili chonse kapena kulowa pa chipata cha sukulu ili yonse.

Koma mbale wamkulu anapita ku mnzinda wamkulu ndipo anakhala kwa dzaka ndipo anali atangobwera kumene, choncho mbale wamkuluyu ankaoneka kuti ndi ozindikira m’maso mwa mphwakeyo, ngakhale kuti mbale wamkuluyo sanali ozindikira kwa anthu ena. M’maso mwa mphwakeyo, mbale wamkuluyu ankaoneka opambana amene ankadziwa zonse pa nthawiyo, amene sankasowa kanthu, ndi amene anali ndi dzibakera dzamphamvu. Mbale wamkuluyo anali odzikuza mu chili chonse. Choncho wamng’onoyo anafunsa mkulu wakeyo, “mbale, kodi icho chikunena chiani?” mbale wake wamkuluyo anayang’ana pachikwangwanicho modzikuza, koma sankamvetsetsa zimenezo. Iye anaganiza, “kodi iwe ndi ine tingadziwe chiani pamene amayi athu ndi atate athu sanatitumize ngakhale kusukulu yamkaka?” mbale wankuluyo anayang’ana chikwangwanicho modeka ndikuwerenga mau. Chikwangwanicho chinkanena kuti, “chenjerani ndi moto” ndipo chinali ndi mau atatu. Mwachidziwikire anthu amene sanaphunzire amaphunzira mwachangu mwanjira ili yonse, ndipo izi zinali choncho ndi mbale wamkulu. Kenako mbale wamkuluyo anauza mphwakeyo, “mphanga bwerezanso. Chikunena kuti ‘mtengo wa magetsi.’ Chikwangwanichi chikunena kuti ndi mtengo wa magetsi.” Mphwakeyo anaganiza, “ah. Mkulu wanga ndipali! ndikuchita manyazi chifukwa sindinaphunzire kulemba ndi kuwerenga, koma ndiyenera kuphunzira mau awa ‘mtengo wa magetsi’ tsopano poti mkulu wanga wandiuza molondola.” Iye anawerenga mau ndipo mauwo anagwirizana ndi mau oti, “mtengo wa magetsi.”

Pamene iwo anali kupitilira ndi ulendo wao china chake chinaoneka. Nthawiyi chikwangwani chinkanena kuti, “khalani osamala ndi moto.” Choncho wamng’onoyo mkulu wakeyo kachiwiri zomwe chikwangwanichi chinkatanthauza poti chinali ndi malemba anayi tsopano. Iye anafunsa, “mbale, kodi ichi chikunena chiani?” mkulu wakeyo anaganiza, “oh icho? Chikunena kuti, ‘mtengo wa magetsi wachiwiri.’” Iye anawerenga mau ndipo anagwirizana. Iye anauza mphwakeyo modzikuza, “mphwanga, bwereza zomwe ndanena.” “mtengo wa magetsi wachiwiri.” Kodi ukumvetsetsa? Kodi unaonanso mtengo wamagetsi oyamba, si choncho? Choncho uwu ndi wachiwiri. Ndipo ichi chikunena kuti ‘mtengo wa magetsi wachiwiri.’ “Kodi izi ndi zolondola kapena ai?” mphwakeyo anadzimva kukula ndi kuganiza, “ah, mkulu wanga ndi osangalatsa.” Ndipo iwo ankapitiliza kunena kuti “mtengo wa magetsi wachiwiri,” “mtengo wa magetsi wachiwiri,” “mtengo wa magetsi wachiwiri” komanso “mtengo wa magetsi wachiwiri,” mpaka pamene mtengo wina wa magetsi unaonekera.

Pamene iwo ankapitiliza kukwera phiri, panali mtengo wina wa magetsi komanso chikwangwani china. Kodi chikwangwanichi chikunena chiani tsopano? Chili ndi mau asanu omwe akuti “chenjerani ndi moto, moto, moto.” Kodi apa akanachita chiani popeza ankayenera kukamba zosiyana ndi “mtengo wa magetsi” pofuna kupanga chofanana? Choncho mbale wamkuluyu anaganiza mosamala ndikunena kuti, “mtengo wa magetsi obwereza wachiwiri,” popeza mtengo wa magetsi unali kuonekera mobwereza bwereza. Iye anauza mphwakeyo kuti, “mphwanga, icho chikunena kuti ‘mtengo wa magetsi obwereza wachiwiri.’” Mbale wakeyo anawerenga mau ndi zala zake ndikuganiza, “‘mtengo wa magetsi obweretsa  wachiwiri’ ndizofanana eti. Ah. Mkulu wanga ndi patali.”

Choncho iwo anapitiliza kukwera phiriro ndipo mtengo wina wa magetsi unaonekera. Kodi chomwe chinali pamtengo wa magetsiwo ndi chiani tsopano? Chikunena kuti, “chenjerani ndi moto usiku ndi usana,” ndipo mbale wamkuluyo anauza mphwakeyo kuti, “mtengo wa magetsi obwereza kachiwiri ndi kachiwiri.”

Kumene iyi ndi nkhani yopeka. Koma izi zikutikumbutsa ife ziphunzitso zonse zopusa za aphunzitsi onyenga zomwe zikunena kuti munthu amalandira chikhululukiro cha machimo popemphera mapemphero akulapa. Abusa akhungu auzimu amaphunzitsa mpingo wao mwachidziwitso popanda kudziwa choonadi. M’maso mwa okhulupilira ao abusa a khungu a uzimuwa amaoneka monga anthu akulu akulu a chikhulupiliro amene akudziwa chili chonse. Okhulupilira amafunsa abusa otere, “abusa, kodi ndingachite chiani popeza ndili ndi tchimo? Ndi mapemphera mapemphero akulapa tsiku ndi tsiku chifukwa ndili ndi tchimo ndipo ndayesera molimba kukhala osachita tchimo, koma ndindakali ndi tchimo. Choncho, kodi ndiyenera kuchita chiani pa tchimoli?” ndipo abusa achinyengowa amawauza iwo, “lapani” ndipo ngati izi sizinakwanire, iwo amawauza kupemphera ndi kusalakudya kwa masiku ambiri, ndipo ngati izi sizinakwanire, iwo amawauza kuti afune fune Mulungu ndi mtima onse popemphera ndi kusalakudya kwa masiku makumi anayi. Iwo amasintha mitu ya mapemphero, ndipo nthawi zonse amauza mpingo wao kuti udzipemphera mapemphero akulapa.

Iwo amanena kuti, “chifukwa chakuti simunapemphere mapemphero akulapa mokwanira. Chifukwa chake simunapemphere ndi kusalakudya monga nsembe yanu yamasiku onse ya kupembedza. Chifukwa chake simunapemphere mapemphero a usiku onse mokwanira.” Choncho iwo amapemphera usiku onse, kupemphera mapemphero akulapa usiku onse la chisanu, kubwera molawila kukachisi la Mulungu mapemphero a m’mawa komanso mapemphero akulapa kwamaola makumi atatu asanayambe utumiki, ndi kupempheranso mapemphero akulapa mukati mwa utumiki wamadzulo, kupemphera mapemphero akulapa mbanda kucha, ndipo iwo amakhala pamodzi m’mapempherowa akulapa. 

Chiphunzitso cha chiyeretso chinachokera kuziphunzitso zimenezi. Chiphunzitso cha chiyeretso chimanena kuti munthu amasintha pang’ono pang’ono ndipo kuti munthu sakhalilatu opanda tchimo chifukwa choti iye amakhulupilira mwa Yesu. Koma malembo akutiuza ife poyera kuti Yesu anachotsa machimo athu onse kamodzi kokha. Yesu anachita zimenezi kamodzi kokha! Koma iwo amanena kuti Yesu analandira ubatizo chifukwa Iye anali munthu odzichetsa. Koma izi zili chonchi chifukwa cha kusadziwa kwao chimene Yesu anabatizidwira. Koma ndiuzeni ine, kudzichepetsa kotani? Kodi Iye anadza pa dziko lino kudzaonetsa kudzichepetsa Kwake? Ai, sichoncho. Ataphunzira ku masukulu a seminale, awo amene akuti ndi abusa ndi atumiki amaphunzitsa mpingu wao kupemphera mapemphero akulap popanda chifukwa cheni cheni ngakhale kuti iwo sanalandire chikhululukiro cha machimo.

Abusa achinyengowa akhala atumiki a chikhulupiliro chanu. Iyi ndi nkhani ya moyo ndi imfa. Ndikunenanso mobwereza; iyi ndi nkhani ya moyo ndi imfa. Kwa anthu amene ali mbuli za uzimu, abusa a chinyengowa amaphunzitsa iwo zomwe zalembedwa pachikwangwani, “mtengo wa magetsi,” koma anthu ophunzira awa adzakana ndikunena kuti, “ai, ukulakwitsa. Kodi chinganene bwanji kuti ‘mtengo wa magetsi’? chikunena kuti, ‘chenjerani ndi moto.’ Nanga izi zikunena bwanji kuti ‘mtengo wa magetsi wachiwiri’? chikunena kuti, ‘chenjerani ndi moto oopsa.’ Kodi chinganene bwanji kuti, ‘mtengo wa magetsi obweretsa kawiri ndi kawiri’? chikunena kuti, ‘chenjerani ndi moto usiku ndi usanu.’” Chonchi atsogoleri a zipembedzowa mu Chikristu aphatikiza phunziro la mapemphero akulapa a okhulupilira ao kwa dzaka zambiri. Ndipo iwo akupitiliza kuwazunza ndi Lamulo ponena kuti, “kodi simunachite machimo mulungu wapitawu? Tiyeni tipemphere mapemphero akulapa tisanayambe utumiki wathu.” Iwo amalamula okhulupilira ao olema kuti apemphere mapemphero akulapa nthawi zonse pamene iwo akumana.

Kodi Yesu ndindani? Yesu anasambitsa mapazi a Petro. kodi chifukwa chiani Yesu anasambitsa mapazi a Petro? Yesu anasambitsa mapazi a Petro kuti iye asanyengedwe ndi mdierekezi. Kwalembedwa mu 1 Petro 3:21, “cimenenso cifaniziro cace cikupulumutsani tsopano, ndico ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lace la thupi komatu funso la cikumbumtima cokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Kristu.” Akunena kuti madzi ndi chifaniziro chimene chikupulumutsa inu mwa kuuka kwa Yesu Kristu. Kodi chifanizirochi ndi chiani? Zikutanthauza kuti china chake mwa chithunzi thunzi kapena chidziwitso chozindikiridwa monga chinthu cheni cheni m’Chipangano Chatsopano chomwe ndi cheni cheni cha m’Chipangano Chakale. Mwachidule ndi chikhazikitso cheni cheni.

Yesu anachotsa machimo athu onse pa thupi Lake mwa kulandira ubatizo, choncho kufa kwake pamtanda chinali chilango cha machimo athu. Madzi a Yesu  ndi chifaniziro chomwe chipulumutsa ife tsopano, ndiko kunena kuti, ubatizo Wake; ndipo inu ndi ine talandira chikhululukiro cha machimo athu pokhulupilira kuti Yesu anachotsa machimo athu onse mwa kulandira ubatizo.  

Choncho utumiki uwiriwu wa Yesu wakwaniritsa chitetezero cha machimo athu: 1 Yohane 5:5-7 akutiuza ife kuti kunakwaniritsidwa mwa madzi ndi mwazi. Akutiuza ife kuti osati mwa madzi okha kapena mwa mwazi okha, koma kunakwaniritsidwa mwa madzi, mwazi ndi Mzimu: Yesu Mulungu weni weni anadza pa dziko lino mu thupi la munthu ndi kulandira ubatizo Wake komanso kulandira chilango chonse pamtanda, kuti ife atipatse ufulu wokhala ana ake, kwa iwo onse amene akhulupiliradi mu zimenezi. Kodi izi zinalembedwa m’malembo kapena ai? Indedi zinalembedwa m’malembo. 

Tiyeni tsopano tiwerenge 1 Petro 1:22-25 pamodzi, “Popeza mwayeretsa moyo wanu pa kumvera coonadi kuti mukakonde abale ndi cikondi cosanyenga, mukondane kweni kweni kucokera kumtima; osati ndi beu yofeka komatu, yasaola mwa Mau a Mulungu amoyo ndi okhalitsa. Popeza anthu onse akunga udzu, ndi ulemerero wao wonse ngati duwa la udzu. Udzuwo ungotota, ndi duwa lace lingogwa; koma Mau a Mulungu akhala chikhalire. Ndipo Mau olalikidwa kwa inu ndi awo.” 

Okondedwa okulupilira anzanga, kodi ‘Mau’ mu ndiime ili pamwamba ndi Uthenga Wabwino kapena ai? Akutanthauza Uthenga Wabwino. Uwu ndi Uthenga Wabwino omwe wapulumutsa ife. Kodi Mau a Mulungu amenena kuti anatipulumutsa ife  mwakulandira ubatizo, kapena ai? Iwo indedi amatero. Mwapeza chipulumutso ngati mwakhulupilira mu Mau amenewa. Kodi mukukhulupilira?  Mwabadwa mwatsopano ndi mbeu yasaola, ndipo osati mwa kudzimva, ndipo osati mwa chifuniro chanu. Nanga kodi tabadwa bwanji mwatsopano? Tabadwa mwatsopano mwa Mau. Tabadwa mwatsopano, osati ndi mbeu yofeka koma yosafeka, kudzera mu Mau a Mulungu amene akukhala kwamuyaya. Ndipo Mau amenewa ali ndi ife nthawi zonse. Iwo akutiuza kuti Mau a Mulungu apulumutsa ife kotheratu.

Kunalembedwa, “Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wace, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi cisomo ndi coonadi” (Yohane 1:14). Mau a Mulungu akunena kuti Ambuye anatipulutsadi ife mwa madzi, omwe ndi, ubatizo wake ndi mwazi Wake pamtanda. Talandira chipulumutso mwa kukhulupilira mu Mau. Kodi mukukhulupilira mu Mau?

Tiyeni tione Buku la Tito 3:5: “Zosati zocokera m’nchito za m’cilungamo, zimene tidazicita ife, komatu monga mwa cifundo cace anapulumutsa ife, mwa kutsuka  kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera, amene anatsanulira pa ife mocurukira, mwa Yesu Kristu Mpulumutsi wathu; kuti poyesedwa olungama ndi cisomo ca Iyetu, tikayesedwe olowa nyumba monga mwaciyembekezo ca moyo wosatha.” 

Kwalembedwa apa mu Buku la chitatu mu ndime yachisanu, “Zosati zocokera m’nchito za m’cilungamo, zimene tidazicita ife, komatu monga mwa cifundo cace anapulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera.” “kubadwanso” uku kukutanthaunza kubadwadi mwatsopano. Ambuye anatipanga ife kubadwa mwatsopano monga woyera mtima olungama chifukwa Iye anatiyeretsa ku machimo athu onse mwa ubatizo Wake. Mulungu anapanga ife atsopano chifukwa kunalembedwa, “mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera.” Mulungu anapanga inu ‘olungama.’ Mulungu anapanga munthu ali yense olungama pamaso Pake. Kukhulupilira mu chilungamo cha Mulungu ndiye chipulumutso. Kukhulupilira mu chilungamo cha Mulungu m’malo modzikuza ndi chilungamo cha munthu- ndi chipulumutso choonadi.

Tiyeni tione Mau ochokera mu Buku la Ahebri 10:9-18: “pamenepo anati, Taonani, ndafika kudzacita cifuniro canu. Acotsa coyambaco, kuti akaike caciwirico. Ndi cifuniro cimeneco tayeretsedwa mwa copereka ca thupi la Yesu Kristu, kamodzi, kwatha. Ndipotu wansembe ali yense amaima tsiku ndi tsiku, naturukira, napereka nsembe zomwezi kawiri kawiri, zimene sizikhoza konse kucotsa macimo; koma Iye, m’mene adapereka nsembe imodzi nsembe imozi cifukwa ca macimo, anakhala pa dzanja lamanja la Mulungu cikhalire; kuyambira pomwepo alindirira, kufikira adani ace aikidwa akhale mpando ku mapazi ace. Pakuti ndi cipereko cimodzi anawayesera angwiro cikhalire iwo oyeretsedwa. Koma Mzimu Woyeranso acitira umboni; pakuti adatha kunena: Ici ndi cipangano ndidzapangana nao, atapita masiku ajawo, ananena Ambuye: Ndidzapereka malamulo anga akhale pamtima pao; ndipo pa nzeru zao ndidzawalemba; ndipo macimo ao ndi masayeruziko ao sindidzawakumbukilanso. Koma pomwe pali cikhululukiro ca macimo palibenso copereka ca kwa ucimo.” 

Akunena mu ndime 18, “Koma pomwe pali cikhululukiro ca macimo palibenso copereka ca kwa ucimo.” Ndipo iyi ikutanthauza kuti palibenso chifukwa kwa ife choperekera nsembe ya machimo athu. Yesu Mwana wa Mulungu anadza pa dziko lino kudza chita chifuniro cha Mulungu. Malembo akuti “Pakuti ici ndi cifuniro ca Mulungu, ciyeretso canu” (1 Atesalonika 4:3). Yesu analandira ubatizo m’malo mwathu ndi kufa pamtanda pofuna kutipanga ife opanda tchimo. Kwalembedwanso, “Acotsa coyambaco, kuti akaike caciwirico” (Ahebri 10:9). Chiyeretso choonadi sichikwaniritsidwa mwa Lamulo, mwakupemphera mapemphero akulapa, mwa mphamvu za munthu, mwa ntchito za bwino kapena mwa chili chonse cha chifuniro cha munthu. Sichingakwaniritsidwe ngakhale mwakupereka kachiwiri moyo wako. Koma Yesu payekha anakwaniritsa chiyeretso choonadichi. 

Iye anachotsa nsembe yoyamba chifukwa chiyeretso sichikanapezeka mwa Lamulo, kapena mwa ntchito za bwino ndi mwa mphamvu za munthu. Choncho kodi Iye anachita chiani? Yesu anapanga ife ‘oyeretsedwa’ mwa chipulumutso Chake. Kwalembedwa, “Ndi cifuniro cimeneco tayeretsedwa mwa copereka ca thupi la Yesu Kristu, kamodzi, kwatha.” “tayeretsedwa” zikutanthauza kuti talandira chikhululukiro cha machimo. Ife tachilandiradi. Izi zikutanthauza kuti, “mwa chifuniro chimenecho Yesu Kristu afufuta machimo athu onse kamodzi kokha ndipo ife amene takhulupilira talandira chipulumutso kamodzi kokha mwa chikhulupiliro kudzera mu nsembe ya thupi ya Yesu Kristu kamodzi kokha.” Okondedwa okhulupilira anzanga, kodi mwachilandira? Kodi mudzachilandira? Kapena mwachilandira? Mwachilandira ngati mwangokhulupilira mu Uthenga Wabwinowu wa choonadi.

Okondedwa okhulupilira anzanga, munali ndi tchimo poyamba sichoncho? Koma, icho sichinali chipulumutso choonadi. Mulungu akuitana a ntchito m’munda Mwake kuti agwire ntchito zosiyana siyana, ndipo pali ena amene anadza kuma 9 mwa mawa ndipo ena masana, ndipo ena anadza ngakhale ku ma 5 kumadzulo, pamene ntchito inali pafupi kutha. Koma ndi chiani chinachitika kwa iwo. Onse analandira mphotho zofanana. Okondedwa okhulupilira anzanga, ngakhale tinayamba kukhulupilira mwa Yesu pamene tinali ndi chaka chimodzi, pamene tinali m’mimba ya amayi athu, pamene tinali ndi dzaka makumi awiri, pamene tinali ndi dzaka makumi asanu ndi chimodzi; tanthauzo lake loonadi ndi lakuti Ambuye anapanga ife okhulupilira mwa Yesu kulandira chinthu chimodzi chimenechi, ‘chipulumutso choonadi.’ Kaya takhulupilira mwa Yesu kwa dzaka khumi ndi mazana adzaka, izo sizingatipangitse ife kukhala olungama pamaso pa Mulungu. Iye wapulumutsa ife mwa ngwiro kamodzi kokha. Talandira chipulumutso mwa kukhulupilira kuti Ambuye wathu anapulumutsa ife kotheratu. Okondedwa okhulupilira anzanga, ndikufunitsitsadi inu kuti mukhulupilire mu zimenezi.

Kodi Kristu anapereka nsembe yamuyaya ku machimo, kapena ai? Yesu Kristu anachotsa machimo onse a dziko mwa kulandira ubatizo ndi kunyamula machimowo kupita nao pamtanda. Ndipo Iye anafa pamtanda atatha kunena kuti “kwatha.” Iye anakwaniritsa chilungamo chonse kamodzi kokha. Mwa masiku atatu pamene Iye anafa pamtanda, Yesu anauka ndi kuchitira umboni kwa masiku makumi anayi, ndipo Iye tsopano wakhala kudzanja la manja la mpando wa Mulungu Atate. Iye choncho sakugwiranso ntchito ili yonse pamene Iye wakhala ku dzanja la manja la mpando wa Mulungu. Iye tsopano sakugwiranso ntchito yochotsa machimo. Iye sakufufutanso machimo chifukwa Iye anafufuta kale machimo onse kamodzi kokha.

Ife tsopano tiyenera kugwira ntchito kuchokera ku umunthu wathu. Kodi ndi ntchito yotani imene tiyenera kuchita? Ife tiyenera kugwira ntchito yokhulupilira. Talandira chipulumutso kwa Mulungu tsopano mwa kukhulupilira muchipulumutso chomwe Yesu anakwaniritsa kamodzi kokha. Ndi mwa chikhulupiliro! Okondedwa okhulupilira anzanga, kodi mukukhulupilira? Yesu sangapatse inu chikhululukiro cha machimo tsiku ndi tsiku. Kuyesera kulandira chikhululukiro cha machimo tsiku ndi tsiku ndi modzi modzi kupachika Yesu pamtanda tsiku ndi tsiku. Ngati mukunena kuti mudakali ndi uchimo ngakhale mwakhulupilira mwa Yesu, ndiye kuti mukumunyoza Iye. Ili ndi tchimo lonyozera Mzimu Woyera.

Kwalembedwa, “Ici ndi cipangano ndidzapangana nao, atapita masiku ajawo, ananena Ambuye: Ndidzapereka malamulo anga akhale pamtima pao; ndipo pa nzeru zao ndidzawalemba.” Tsopano, kodi mwalandira chikhululukiro cha machimo anu? Kodi mukukhulupilira  mu Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu? Kodi muli ndi tchimo kapena mulibe tsopano? Tsopano ndikufuna inu muganize mwakuya pa zimenezi. Kodi mukuganiza kuti muli ndi tchimo kapena ai? Mulibe tchimo, mukugwirizana nazo? Kodi muli ndi tchimo kapena mulibe tchimo mu mtima mwanu? Mulibe katchimo kali konse mu mtima mwanu. Kodi mungakhale bwanji ndi tchimo pamene machimo anu onse anaperekedwa pa Yesu? Kodi mungakhale bwanji ndi machimo pamene anaperekedwa kale? Izi  ndi zoona.

Patatha tsiku lomwe ndinakhulupilira mu chikhululukiro cha machimo, pamene ndinakhulupilira kuti machimo anga anaperekedwa pa Yesu mwa ubatizo Wake, ndipo kuti Yesu anafa pamtanda, kuti Iye anafa m’malo mwanga, komanso kuti Iye anaukitsidwa m’malo mwanga; kenako Ambuye Mulungu ananenanso kwa ine, “Ndidzapereka malamulo anga akhale pamtima pao; ndipo pa nzeru zao ndidzawalemba.” Nanga, kodi Lamulo la Mulungu ndi chiani? Ndi Lamulo la chikondi. Ndi Lamulo lonena kuti, “ndakupulumutsani inu.” Choncho tsopano ndinganene kuti, “Ambuye, mwandipulumutsa ine kudzera mwa madzi ndi wazi.” Kodi inu mumakhulupiliranso zimenezi mu mtima mwanu? Akunena kuti Mulungu adzalemba zimenezi mumaganizo mwao. Kodi izi tsopano zinalembedwa mu mtima mwanu? Uwu ndi Uthenga Wabwino wakale. Ndikufuna inu mugonjetse dziko lino ndi kulandira chipulumutso mwa kukhulupilira mu Uthenga Wabwinowu.

Kuchitira umboni madzi a ubatizo omwe Yesu analandira ndi mwazi Wake pamtanda komanso Ambuye, pamene anauka kwa akufa ngati Ambuye wathu ndi wakale kapena Uthenga Wabwino oyamba. Chikhulupiliro chokhacho chomwe chingagonjetse dziko lino ndi chikhulupiliro chokhulupilira mu Uthenga Wabwino wakale kapena oyamba.