Sermons

【3-16】< Yohane 13:1-17 > Uthenga Wabwino Wa Chitetezero Omwe Wafufuta Machimo Anu Onse a Masiku Onse< Yohane 13:1-17 >

“Koma pasanafike phwando la Paskha, Yesu, podziwa kuti nthawi yace idadza yakucoka kuturuka m’dziko lino lapansi, kunka kwa Atate, m’mene anaconda ace a Iye yekha a m’mdziko lapansi, anawakonda kufikira cimariziro. Ndipo pokhala pamgonero, mdierekezi adatha kuika mu mtima wace wa Yudase mwana wa Simoni Isikariote, kuti akampereke Iye, Yesu, podziwa kuti Atate adampatsa Iye zonse m’manja mwace, ndi kuti anacokera kwa Mulungu, namuka kwa Mulungu, ananyamuka pa mgonero, nabvula Malaya ace; ndipo m’mene adatenga copukutira, anadzimanga m’cuuno. Pomwepo anathira madzi m’nsambidwe, nayamba kusambitsa mapazi a akuphunzira ace, ndi kuwapukuta ndi copukutira, cimene anadzimanga naco. Anadza pomwepo kwa Simoni Petro. Iyeyu ananena ndi Iye, Ambuye kodi Inu mundisambitsa ine mapazi? Yesu anayankha nati kwa iye cimene ndicita Ine, sucidziwa tsopano; koma udzadziwa m’tsogolo mwace. Petro ananena ndi Iye, simudzasambitsa mapazi anga ku nthawi yonse. Yesu anamyankha iye, Ngati sindikusambitsa iwe ulibe colandira pamodzi ndi Ine. Simoni Petro ananena ndi Iye, Ambuye si mapazi anga okha, komanso manja ndi mutu. Yesu ananena naye, Amene anatha kusamba alibe kusowa koma kusamba mapazi, koma ayera monse: ndipo inu oyera, koma si nonse ai. Pakuti anadziwa amene adzampereke Iye; cifukwa ca ici anati, simuli oyera nonse. Pamenepo, atatha Iye kusambitsa mapazi ao, ndi kutenga Malaya ace, anaseamanso, nati kwa iwo, Nanga cimene ndakucitirani inu, mucizindikira kodi? Inu mundicha Ine Mphunzitsi, ndi Ambuye: ndipo munena bwino; pakuti ndine amene. Cifukwa cace, ngati Ine Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsa mapazi wina ndi mnzace. Pakuti ndakupatsani inu citsanzo, kuti, monga Ine ndakucitirani inu, inunso mucite. Indetu, indetu, ndinena inu, Kapolo sali wamkulu ndi Ambuye wace; kapena mtumwi Sali wamkuru ndi womtuma iye. Ngati mudziwa izi, odala inu ngati muzicita.”Ndi chifukwa chiani Yesu anasambitsa mapazi a Petro pa Paskha? Pamene ankasambitsa mapazi a Petro, Yesu anati kwa iye, “cimene ndicita Ine, sucidziwa tsopano; koma udzadziwa m’tsogolo mwace.” Petro anali mtumwi oyambilira wa Yesu. Iye anakhulupilira mwa Yesu monga Mwana wa Mulungu, ndipo iye anabvomereza kwa Yesu, “Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu” (Mateyu 16:16). 

Payenera kukhala chifukwa chomwe Yesu anasambitsira mapazi a ophunzira Ake. Pamene Petro anabvomereza kuti Yesu anali Kristu, iye ankaulula chikhulupiliro, kuchitira umboni kuti Yesu anali Mpulumutsi amene anatetezera machimo onse.

Chifukwa chiani Yesu anasambitsa mapazi a Petro? Chifukwa choti Yesu anadziwa kuti Petro adzamukana Iye katatu. Mwanjira ina, Iye anadziwa kuti Petro adzachitanso tchimo pamaso pa Ambuye. 

Ngati tchimo lina lake latsalila mu mtima mwake Ambuye atakwera kumwamba, kukanakhala kobvuta kuti iye apange ubale ndi Ambuye. Koma Ambuye anadziwa kufooka kwa ophunzira Ake, ndipo Iye sanafune kuti iwo asakhale pa mtendere pakati pa ubwenzi wao ndi Ambuye chifukwa cha machimo ao. Choncho Ambuye anafuna kuwaphunzitsa iwo kuti Iye watsuka kale machimo ao a masiku onse. Ichi ndi chifukwa chake Yesu anasanmbitsira mapazi a ophunzira Ake. Ngakhale Iye asanafe pamtanda, Yesu anawaphunzitsa iwo Uthenga Wabwino wa Ubatizo Wake, kufotokoza kwa iwo kuti Iye wapulumutsa iwo mwa ngwiro ngakhale ku machimo ao amtsogolo.

Yohane 13 akufotokoza Yesu akuuza ophunzira za chipulumutso chathunthu chotsiriza. Pamene akutsuka mapazi a ophunzira, Yesu akufotokoza kwa iwo Uthenga Wabwino wa nzeru ya ubatizo Wake omwe unapanga kuthekera kwa iwo kuti atsukidwe ku machimo ao onse a masiku onse, kunena kuti, “musanyengedwe ndi satana. Ndinasenza machimo anu onse mwakubatizidwa ndi Yohane Mbatizi mu mtsinje wa Yordano, ndipo ndidzaweruzidwa kamba ka machimo anu onse pamtanda ndi kuukanso kwa akufa kumaliza chipulumutso chanu komanso chikhululukiro cha machimo anu. Ndikusambitsa mapazi anu ndi sanafe pamtanda kuti ndikuphunzitseni Uthenga Wabwino wa choonadi wa chitetezero cha machimo, kukuuzani kuti ndatsuka kale machimo anu onse amasiku onse. Ichi ndi chinsinsi cha Uthenga Wabwino wakukonzedwanso omwe watsika inu ngakhale machimo a masiku onse. Khulupilirani mu Uthenga Wabwinowu.”

Tiyenera kumvetsetsa apa chifukwa chimene Yesu anasambitsira mapazi a ophunzira, komanso kudziwa chifukwa chimene Ambuye ananena kuti, “cimene ndicita Ine, sucidziwa tsopano; koma udzadziwa m’tsogolo mwace.” Ndipo onse a ife tiyenera kupulumutsidwa mwa kukhulupilira mu Uthenga Wabwino wakukonzedwanso.Pofuna Kuti Ophunzira Adziwe Chitetezero Cha Machimo Onse a Masiku Onse


Asanafe pamtanda, Yesu anali ndi chakudya cha madzulo ndi ophunzira, ndipo pamenepo Iye anasambitsa mapazi a ophunzira kuwaphunzitsa iwo Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo.

Kwalembedwa, “Yesu, podziwa kuti Atate adampatsa Iye zonse m’manja mwace, ndi kuti anacokera kwa Mulungu, namuka kwa Mulungu, ananyamuka pa mgonero, nabvula Malaya ace; ndipo m’mene adatenga copukutira, anadzimanga m’cuuno. Pomwepo anathira madzi m’nsambidwe, nayamba kusambitsa mapazi a akuphunzira ace, ndi kuwapukuta ndi copukutira, cimene anadzimanga naco. Anadza pomwepo kwa Simoni Petro. Iyeyu ananena ndi Iye, Ambuye kodi Inu mundisambitsa ine mapazi? Yesu anayankha nati kwa iye cimene ndicita Ine, sucidziwa tsopano; koma udzadziwa m’tsogolo mwace.” Yesu anauza ophunzira Ake za Uthenga Wabwino wa ubatizo Wake, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo.

Petro ankakhala moyo wake wa chikhulupiliro popanda kuzindikira chifuniro cha Ambuye, choncho iye sakanatha kumvetsetsa chifukwa chomwe Yesu anafunira kutsuka mapazi ake. Komabe, pamene Yesu analankhula kwa iye, chikhulupiliro cha Petro chinasintha. Ambuye anafuna kuuza Petro za Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, Uthenga Wabwino wa za ubatizo Wake. Yesu anakhudzika kuti pamene Petro adzachita machimo amasiku onse mu thupi, iye angatembenuke ndikukhala okhulupilira ochimwa kulephera kuyandikana ndi Yesu chifukwa cha machimo. Ichi ndi chifukwa chake Yesu anasambitsa mapazi a Petro, kuti iye asagwere mu msampha umenewu. Mwanjira ina, Ambuye anatsuka mapazi a ophunzira kuti mdierekezi asatenge chikhulupiliro chawo. Koma Petro anazindikira izi pambuyo pake chifukwa chimene Yesu anasambitsira mapazi ake. 

Yesu anapanga kuthekera kwa ali yense amene wakhulupilira mu ubatizo Wake ndi mwazi kulandira chikhululukiro chosatha cha machimo. Zomwe Yesu akunena apa mu Yohane 13 pamene akutsuka mapazi a ophunzira ndi zofunika kwambiri moti zingamveka pokhapo ngati munthu wabadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Yesu anatsuka mapazi a ophunzira Ake pachikondwerero cha Paskha kuti iwo azindikire Iye asanafe pamtanda kuti Iye watsuka machimo onse a dziko kuphatikiza machimo ao onse a masiku onse. Iye ankanena kuti, “suchidziwa tsopano chifukwa chimene ndikutsukira mapazi ako. Koma ukazazindikira kuti ndinasenza machimo ako onse mu mtsinje wa Yordano mwa ubatizo Wanga, uzazindikira chifukwa chomwe ndikutsukira mapazi ako.” Zomwe Yesu ananena kwa Petro pa tsiku la Paskha ndi choonadi cha kusinthidwa.

Tiyenera kumvetsetsa ndi kukhulupilira mu ubatizo wa chitetezero cha machimo omwe watsuka ife kotheratu ku machimo athu onse a masiku onse. Ubatizo omwe Yesu analandira mu mtsinje wa Yordano ndi omwe unali kuika manja, mwambo omwe Yesu anatengera machimo athu onse. Tiyenera kukhulupilira mu Mau a chitetezero cha machimo, onena kuti Yesu anachotsa machimo onse a dziko mwakubatizidwa ndipo Iye anaweruzidwa chifukwa cha machimowo pamtanda. Pofuna kufufuta machimo onse a mtundu wa anthu, Ambuye anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi pa thupi Lake, ndipo Iye indedi anapukuta machimo onse a dziko lapansi. Chitetezero Cha Machimo a Masiku Onse Chakwaniritsidwa Kudzera Mu Ubatizo Ndi Mwazi Wa Yesu


Yesu anadziwa bwino lomwe kuti pamene Iye adzafa pamtanda, kuuka kwa akufa, ndi kukwera kumwamba, satana ndi aneneri ake onyenga adzayesera kunyenga ophunzira kuti ayang’ane pa mwazi okha wa Yesu wa pamtanda. Ngakhale, pamene tikuona kubvomereza kwa chikhulupiliro cha Petro, pomwe ananena kuti “Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu,” tikuona kuti Petro anakhulupilira mwa Ambuye ndi mtima wake onse. Komabe, kunali Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo omwe Yesu ankafuna kuphunzitsa Petro. Uthenga Wabwinowu unali ubatizo omwe Yesu analandira pofuna kuchotsa machimo onse a dziko lapansi mu mtsinje wa Yordano. Yesu anafuna kuphunzitsa ubatizowu kachiwiri kwa Petro, kwa ophunzira onse, komanso mbadwo wa kutsogolo omwe ukudza, kuphatikizanso ife. Choncho Iye anati, “cimene ndicita Ine, sucidziwa tsopano; koma udzadziwa m’tsogolo mwace.” 

yesu anadziwa kuti ophunzira Ake azadzipeza okha akuchita tchimo dzaka ziri nkudza, ndipo pa nthawi ili yonse yotere satana adzaweruza iwo ndi kuwaimba mlandu, kuyesa kuwanyenga iwo ponena kuti, “kodi mungakhale bwanji opanda tchimo pamene mukuchimwa chotere? Simunapulumutsidwe. Mudakali ochimwa!” Choncho, pofuna kuteteza ophunzira ku nsampha otere, Yesu anawauziratu iwo kuti monga m’mene akutsukira mapazi ao ndi madzi, iwo adzatsuka machimo ao amasiku onse mwa kukhulupilira mu ubatizo Wake.

Yesu ankanena kwa iwo, “inu mukudziwa kuti Ine ndabatizidwa chifukwa cha inu. Ndinabatizidwa mu mtsinje wa Yordano kutsuka machimo anu onse, achibadwidwe komanso amasiku onse pamodzi. Kodi mukumvetsetsa tsopano chifukwa chomwe ndinabatizidwira, komanso chifukwa chomwe ndiyenera kupita pamtanda ndi kukhetsa mwazi wanga mpaka kufa?” Ambuye anatsuka mapazi a ophunzira kuwaphunzitsa iwo kuti Iye anasenza machimo ao onse amasiku onse kudzera mu ubatizo Wake, ndipo kuti Iye adzathetsa machimo ao onse mwa kuweruzidwa pamtanda m’malo mwao.

Tsopano, inu ndi Ine talandira chikhululukiro cha machimo mwa kubatizidwa mu Uthenga Wabwino wa ubatizo wa Yesu omwe wapanga chitetezero cha machimo. Kuchipulumutso chathu, Yesu anabatizidwa kunyamula machimo athu mu mtsinje wa Yordano, ndipo Iye anapachikidwa mpaka kufa. Ndi ubatizowu omwe Ambuye analandira kuti anyamule machimo onse, komanso mwazi omwe Iye anakhetsa kupereka mphotho ya machimo, Iye anafufuta machimo athu onse. Ali yense amene wamvetsetsa Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo ndi kukhulupilira mu choonadichi adzachotseredwa machimo ake onse.

Nanga, kodi tingakhale bwanji moyo wathu wachikhulupiliro pamene tapulumutsidwa? Tiyenera kubvomereza machimo athu a tsiku ndi tsiku, ndipo tiyenera kuzindikira chipulumutso cha ubatizo ndi mwazi wa Yesu, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo. Tiyenera kukhulupilira mu Uthenga Wabwinowu ndikubvomera kuti Yesu wapanga chitetezero cha machimo athu onse kudzera mwa ubatizo Wake ndi mwazi.

Pamene mwachita tchimo kachiwiri mutapulumutsidwa kale, kodi izi zikutanthauza kuti mudzabwereranso kukhala ochimwa kachiwiri chifukwa cha machimo anu a tsiku ndi tsiku? Ai, si m’mene ziriri. Popeza Ambuye anachotsa tchimo lili lonse kudzera mu ubatizo Wake ndi zosatheka kwa ife kukhala ochimwa kachiwiri chifukwa chochita machimo masiku onse. Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo muli ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pamtanda. Ali yense amene wakhulupilira mu Uthenga Wabwinowu wakale wa chitetezero cha machimo mwabadwa mwatsopano kukhala munthu olungama kuchoka ku ochimwa. Olungama Sangakhalenso Ochimwa Kachiwiri


Ngakhale mwakhulupilira mu Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, ndiye mukumva mu mtima mwanu kuti mwakhala ochimwa kachiwiri chifukwa cha machimo anu amasiku onse, ndiye kuti muyenera kubwereranso mu mtsinje wa Yordano momwe Yesu anabatizidwa kuchipulumutso chanu. Kumeneko, muyenera kachiwiri kutsimikiza chikhulupiliro chanu mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, kuzindikira kuti Yesu anasenza machimo onse a dziko kuphatikiza machimo anu onse amasiku onse mwa kubatizidwa ndi Yohane Mbatizi; ndipo kumeneko, muyenera kulingalira pa za Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo kachiwiri, kuganiza za ubatizo wa Yesu ndi mwazi wa Wake, kuika chikhulupiliro chanu mwa izo, ndi kuzindikira Yesu ngati Mpulumutsi wanu ndi kukhulupilira mwa Iye mosanjenjema.

Ngati mwakhulupilira mwa Yesu ngati Mpulumutsi wanu, ndiye kuti mufunika kukhulupilira mu Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo onena kuti machimo anu onse anaperekedwa pa thupi la Yesu kudzera mu ubatizo Wake. Ngati mumakhulupiliradi mu ubatizo wa Yesu, imfa Yake pamtanda, kuuka Kwake, ndipo mwalandira Mau onse a choonadi, ndiye kuti simungakhalenso ochimwa kachiwiri posatengera kuti ndi machimo otani amene mumachita masiku onse, pakuti mwachotseredwa machimo anu onse a dziko mwakukhulupilira mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo.

Ngakhale mwabadwa mwatsopano, timapitiriza kuchimwa chifukwa cha kufooka kwathu, koma Yesu Kristu anasenza kale machimo onsewa mwakubatizidwa ndi Yohane Mbatizi; kudzera mu Uthenga Wabwino wa ntchito ya chitetezero cha machimo, Ambuye anapulumutsa ife kotheratu. Choncho tsopano, kunali kofunika kwambiri kuti Yesu abwere pachimake pakufunika ubatizo Wake kwa ophunzira Ake, ndipo ichi ndi chifukwa chake Iye anasambitsa mapazi ao-ndiko kunena kuti, Yesu anatsuka mapazi a ophunzira kuwakumbutsa iwo za Mau a ubatizo Wake kachiwiri, ndi kubwera pachimake kwa nthawi yomaliza kuti Iye anatsuka machimo ao onse kudzera mu ubatizo Wake, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo. Kunena kwina, Yesu wapanga chitetezero cha machimo onse a mtundu onse wa anthu ndi kupulumutsa ali yense mwa kubatizidwa, kufa pamtanda, kuuka kwa akufa, ndi kukwera kumwamba. Ophunzira Ake onse kenako anali ndi kuthekera kolalikira mpaka pamapeto Uthenga Wabwino wa Yesu, mtanda Wake, kuuka Kwake, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo.Kufooka Kwa Thupi La Petro


Baibulo lalemba kuti pamene Petro ankaimbidwa mlandu okhala otsatira wa Yesu katatu, iye anakana kawiri mwa nthawi yoyamba kunena kuti “ai, izo sizoona! Sindimudziwa munthu ameneyu,” koma mwa nthawi yachitatu, iye sanamkane kokha Yesu koma anamtembereranso Iye.

Tiyeni tibvundukule Mateyu 26:69-75 tiyeni tione zimene Baibulo likunena kweni kweni: “Ndipo Petro adakhala pabwalo: ndipo mdzakazi anadza kwa iye, nanena, Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya. Koma iye anakana pamanso pa anthu onse, kuti, Cimene unena sindicidziwa. Ndipo pamene iye anaturuka kunka kucipata, mkazi wina anamuona, nati kwa iwo a pomwepo, Uyonso anali ndi Yesu Mnazarayo. Ndipo anakananso ndi cilumbiro, kuti, sindidziwa munthuyo. Ndipo popita nthawi yaing’ono, iwo akuimapo anadza, nati kwa Petro, Zoonadi, iwenso uli wa iwo; pakuti malankhulidwe ako akuzindikiritsa iwe. Pamenepo iye anayamba kutemberera ndi kulumbira, kuti, Sindidziwa munthuyo. Ndipo pompo tambala analira. Ndipo anakumbukira mau amene Yesu adati, Asanalire tambala udzandikana katatu. Ndipo anaturukira kunja, nalira ndi kuwawa mtima.”

Petro anakhulupilira mwa Yesu ndi mtima onse ndi kutsata Iye nthawi zonse, podziwa kuti Yesu anali Mulungu Wake, Mpulumutsi Wake ndi m’neneri ali nkudza, pamene Iye anapita kubwalo la Pilato anadzipeza yekha osokonezeka, iye anakana Yesu ndi kumtembelera Iye. Petro sankadziwa kuti iye adzakana Yesu ndi kudzipulumutsa yekha motere, koma Yesu anadziwa kufooka kwake ndi chifukwa chake Ambuye anakamba za Uthenga Wabwino wa chipulumutso kwa Petro pamene ankatsuka mapazi ake, kunena kwa iye mu Yohane 13, “udzachimwa machimo amasiku onse pambuyo pake. Koma ndachotsa kale machimo onsewo.”

Petro anakana Yesu pofuna kupulumutsa moyo wake, koma ili linali tchimo lomwe Petro anachita mwa thupi lake lofooka, ndipo ichi ndi chifukwa chake Yesu anatsuka mapazi ake kumukumbutsa iye kuti Ambuye anapulumutsa ophunzira Ake onse ku machimo ao a thupi. Mwanjira ina, Yesu ankanena kwa ophunzira Ake, “ndidzatsuka machimo onsewa amene mudzachita mtsogolo. Ndachotsa machimo anu onse mwa ubatizo wanga, ndipo ndidzapachikidwa kusenza chilango chonse cha machimo anu. Ndine Mpulumutsi Wanu wa ngwiro, Mulungu wanu komanso Mesiya wanu. Ndine Mbusa wanu amene ndidzapanga chitetezero cha machimo anu onse ndikupulumutsa inu ku machimo onse a dziko mwa ubatizo ndi mwazi. Ndine Mbusa wanu wa chipulumutso.” Kunali kudzala Uthenga Wabwinowu wa choonadi molimba m’mitima ya ophunzira omwe Yesu anatsuka mapazi ao pa phwando la Paskha.

Ngakhale pamene tinalandira chikhululukiro cha machimo, onse a ife tidakali ndi thupi lathu, ndipo choncho ife nthawi zina timachimwa chifukwa cha kufooka kwa thupi lathu. Kumene, tiyenera kuyetsetsa osachita tchimo lili lonse mu thupi lathu, koma kwa nthawi ndi nthawi, pamene tadzipeza tokha mnyengo yobvuta monga Petro, popanda ngakhale kuzindikira timadzipeza tokha tikunama ndi kugwetsedwa chifukwa cha machimo amasiku onse. Umu ndi m’mene tilili kufooka mu thupi lathu. Komabe, ngakhale thupi lathu nthawi zonse ndi lofooka ndipo choncho sitingakwanitse koma kuchimwa pamene tikukhala mu dziko lino, Ambuye anachotsa machimo athu ngakhale kachimo kakang’ono ka ali yense kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi Wake pamtanda, chipulumutso cha chitetezero cha machimo.

Nkhani yomwe ilia pa siyakuti munthu osakhulupilira akukana kuti Yesu ndi Mpulumutsi Wake ai. Koma, ndiyakuti okhulupilira akutsata thupi lake, mwailo tsopano wachita tchimo losemphana ndi chifuniro cha Mulungu. Machimo a munthu amachokera ku zikhumbo za thupi, ndipo choncho Ambuye Yesu anadziwa bwino kuti ndi thupi lomwe anthu amachitira tchimo. Monga Mpulumutsi wathu wa ngwiro, Yesu anapanga chitetezero chokwanira kwa tchimo lili lonse la machimo athu, ndipo ndi ubatizo Wake, mwazi ndi kuuka Kwake, Iye wafufuta machimo onse a dziko. Ntchito ya chipulumutsoyi inakwaniritsidwa kudzera mu ubatizo ndi mwazi wa Ambuye wathu; mwachoyamba, Yesu analandira machimo onse a dziko kuchokera kwa Yohane Mbatizi, ndipo kumapeto, Iye anasenza chiweruzo chonse cha machimowo. Uwu ndi Uthenga Wabwino wa chipulumutso komanso kusinthidwa omwe Ambuye anali nao m’maganizo pamene Iye ananena pamtanda kuti “kwatha” Yohane 19:30.

Petro anamkana Yesu kosachepera katatu, ndipo tingaganize apa m’mene angachitire manyazi ndi kudzipatsa mlandu nthawi zonse pamene iye anamkana Ambuye. Mwa zonse, iye analumbira kuti sadzamkana Yesu. Komabe, monga ali yense, Petro nayenso anali ofooka mthupi, ndipo ichi ndi chifukwa chake iye anachimwa pokana Yesu katatu, ngakhale choncho, kumayenera kukhala kosapilirika kwa Petro akaziyang’ana yekha. Kodi anali wamanyazi chotani Petro pamene iye wayang’ana kwa Yesu pa nthawi? Koma Yesu anadziwa zimenezi poyambilira.

N’chifukwa chake Ambuye ananena kwa Petro, “ndikudziwa kuti iwe udzachitanso uchimo mthupi lako, motero ungadzandime chifukwa cha machimo ako ndikutembenuka kukhala ochimwa kunyalanyaza kuyandikana ndi Ine, ndanyamula machimo ako onse amasiku onse kudzera mu ubatizo wanga. Chifukwa choti ndinabatizidwa, ndizalangidwa chifukwa cha machimo ako, ndikukhala Mbusa wako wa ngwiro. Khulupilira mu Uthenga Wabwino wa machimo ako. Ngakhale umachimwa mthupi lako ndipo waperewera ku ungwiro wanga, ndimakukondabe. Ndinafufuta kale machimo ako ndi ubatizo wanga. Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo ndi Uthenga Wabwino wamuyaya omwe wachotsa machimo ako onse. Chikondi change pa iwe chidzakhalabe chosasintha.”

Yesu analankhula Mau a Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo kwa Petro ndi kwa ophunzira Ake apa mu Yohane 13 chifukwa Uthenga Wabwinowu ndi ofunika kwa ali yense kukhulupilira mwa Yesu ndikubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Ndi chifukwa chake Ambuye ananena kwa iwo, “Ngati sindikusambitsa iwe ulibe colandira pamodzi ndi Ine.”

Tsopano, mu ndime 9 ndi 10 apa, Baibulo likunena kuti, “Simoni Petro ananena ndi Iye, Ambuye si mapazi anga okha, komanso manja ndi mutu. Yesu ananena naye, Amene anatha kusamba alibe kusowa koma kusamba mapazi, koma ayera monse.” 

Kodi mukuganiza kuti mudzapitiriza kuchimwa mthupi lanu mutsogolo, kapena mukuganiza kuti simudzachimwanso? Kumene, mudzachimwanso. Komabe, Ambuye akunena kuti Iye anasenza machimo athu onse kudzera mu ubatizo ndi kutsuka machimo onse kudzera mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo. Iye ananena momveka bwino kwa ophunzira Ake asanafe pamtanda kuti Iye anatsuka tchimo lili lonse la machimo a masiku onse mu dziko lino, ndipo Iye analankhula Mau a Uthenga Wabwino wa choonadi wa chitetezero cha machimo kwa okhulupilira Ake onse. 

Chifukwa kufooka kwa thupi la Petro kulinso ndi ife nthawi zonse, sitingadzitandize koma kuchimwa mu dziko lino. Ndi chifukwa chake, atachotsa machimo onse a ochimwa ali yense mu dziko lino, Ambuye wathu anauza okhulupilira Ake onse kudzera mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo kuti Iye watsuka machimo ao onse ndi ubatizo Wake. Yesu sanatsuke mitu yathu yokha kapena mathupi, koma Iye anatsukanso mapazi athu-ndiye kuti, Iye watsuka ngakhale machimo athu onse amtsogolo. Ndipo uwu ndi uthenga wabwino wa ubatizo wakusinthidwa. Pamene Yesu anabatizidwa, Yohane Mbatizi anachitira umboni, “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” (Yohane 1:29) Muyenera kukhulupilira mu choonadichi, kuti machimo onse a dziko anaperekedwa pa Yesu Kristu ndipo atetezeredwa ndi Iye.

Ali yense amachita tchimo mu thupi pokha pokha ngati iye akukhala mu dziko lino. Tiyenera kubvomereza zimenezi. Pamene kufooka kwathu kwa umunthu kwaonekera monga Petro analili, tiyenera kutsimikiza, kudzera mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, kuti Ambuye wathu anasamala za machimo athu onse mwakubatizidwa mu mtsinje wa Yordano ndi kukhetsa mwazi Wake pamtanda, kutsimikiza chipulumutso choonadichi, kukhulupilira mwa icho, ndi kuyamika Ambuye pa icho.

Tiyeni tsopano tibvomereze chikhulupiliro chathu mu Uthenga Wabwinowu wa ngwiro wa chitetezero cha machimo ndi kunena kwa Ambuye kuti Iye ndi Mpulumutsi wathu komanso Mulungu wathu. Ndikuthokoza Ambuye.Maganizo Oipa Amalingalilo a Munthu


Anthu onse mu dziko lino amachita machimo a ku thupi ndi matupi awo. Chifukwa chakuti iwo anatenga chibadwidwe cha uchimo kwa makolo awo, ena a iwo amakhala moyo wao onse osachita chili chonse koma kuchimwa ndi matupi awo mpaka kufa. Ngakhale ena amachita za bwino ndi matupi awo, koma anthu ambiri m’machitidwe awo ndi oipa.

Yesu ananena mu Mateyu 15:19-20: “Pakuti mumtima mucokera maganizo oipa, zakupha, zacigololo, zaciwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano; izo ndizo zoipisa munthu, koma kudya osasamba ku manja sikuipitsa munthu ai.” Kunena kwina, Mulungu akunena apa kuti muntu ndi onyansa, pakuti muli mitundu khumi ndi iwiri ya machimo onyansa mkati mwa mtima wa munthu (Marko 7:21-23).Ali Yense Ayenera Kubvomereza Kuipa Kwake 


Tisanamvere Mau a Mulungu kuti tibadwe mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu, tiyenera choyamba kuvomereza kwa Mulungu kuti ife tokha ndife ochimwa otheratu ndi kunena kuti, “Ambuye, machimo onsewa ali mkati mwa ine. Ndili ndi khumbo loipa chotere mu mtima mwanga.ndili ndi mitundu khumi ndi iwiri ya machimo yomwe Baibulo likunena.” Komabe, anthu ambiri safuna kuonetsa kuipa kwao. M’malo mwake, amakana ndi kunena kuti, “ndinalibe khumbo lili lonse lochita zomwe ndachitazi. Nzeru zanga zinaperewera chabe ndipo ndalakwitsa moyenera mu chiweruzo changa.”

Koma kodi Mulungu akunena chiani za Munthu? Iye akuneneratu kuti mkati mwa munthu muchoka maganizo oipa, ndipo kuti aliyense zomwe amaganiza moyo wake onse ndi zoipa basi. Nanga maganizo anu bwanji? Kodi ndi oipa kapena abwino? Kodi mukuzindikira kuti maganizo anu onse ndi oipa? Maganizo a munthu indedi ndi oipa monga kwalembedwa, “Ndipo anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukuru pa dziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yao zinali zoipabe zokhazokha (Genesisi).

Zaka zingapo zapitazo, sitolo ina mu Korea inagwa ndipo anthu ambiri ankachotsedwa pansi pa zinyalala. Pamene nkhani inamveka, anthu anathamangira kumaloko kukaona okondedwa awo, koma panalinso owonelera ambiri. Ena a iwo anaganiza, “zatheka bwanji anthu osafa? iwo akunena kuti anthu okwana 200 kapena 300 okha ndi amene anafa, koma izi sizoopsa kwambiri kwa ine. Ndimafuna anthu chikwi akanafa; izo zikanandimvetsa bwino kwambiri.” Muyenera kuzindikira kuipa kwa maganizo a munthu. Ndipo muyenera kuvomereza zimenezi. Ozunzidwa ndi ngoziyo anafa mosayembekezera ndipo mabanja awo anaona miyoyo yao ikuonongeka mosayembekezera, koma pakati pa owonelera, panali ena omwe ankaganiza, “ndimafuna akanafa anthu ambiri! Ndikanakondanso kukanakha zoonongeka zambiri motere. Kodi zimenezi sizikanakhala bwino zikanati zachitikira ku bwalo la masewero? Zikanakhala zokondweretsa kuona bwalo la masewero likuonongeka pamene masewero afika pachimake ndi kuononga anthu ambiri.”

Lolani ndikupatseni chitsanzo china. Ngati mwakumana ndi ngozi ya galimoto pamene mukuyendetsa galimoto munsewu, mudzafuna kuchepetsa liwiro kuti muone chomwe chikuchitika. Koma mukanamva bwanji ngati ngoziyo siinali yaikulu momwe munkaonera? Zoona zake nzakuti, maso anu oipa akanakhumudwa. Choncho mungathe kuona kuipa kwa maganizo amunthu. Kumene, ali yense angadandaule ndi mau okha pamene ngoziyo yachitika, koma mkati mwao, ena amaganiza, “ndikudabwa kuti afa angati. Mazana? Zikwi? Akanafa ambiri zikanandimvetsa bwino!” Izi, okondedwa anzanga okhulupilira, ndiye chilengedwe cha mitima ya anthu. Ali yense ndi oipa chotere asanabadwe mwatsopano?

Tiyen tiwerenge marko 7:20-23 pamodzi. “Ndipo anati, coturuka mwa munthu ndico cidetsa munthu.Pakuti m’kati mwace mwa mitima ya anthu, muturuka maganizo oipa, zaciwerewere, zakuba, zakupha, zacigololo masiriro, zoipa, cinyengo, cinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa: zoipa izi zonse zituruka m’kati, nizidetsa munthu”Khumbo Lakupha mwa Munthu


Mulungu ananena kuti ali yense ali ndi khumbo lakupha mu mtima mwake. Koma anthu ambiri amakana kuzindikira kuti iwi ali ndi kupha mu mtima mwao motero amanena kwa mulungu kuti, “Ndi zopanda nzeru zimenezo! Ndilibe maganizo akupha mpang’ono pomwe! Kodi munganene bwanji zamwano chotere kwa ine?” Pamene anthu oterewa avomereza kuti munthu ndi oipa mwa chibadwidwe, iwo amaganizabe kuti nkhani yosafunikirayi sikhudza iwo. Iwo amati, “sindine oipa kwambiri. Mulungu ankanena dzigawenga zomwe mumamva mu nkhani – ambanda, akupha mwa nkhanza, ogwililira, ndi ena otero, okma osati ine. Ndine osiyana mwachikhalire ndi anthu amenewa. Awa si anthu! Choncho mwaukali amafuula, “tiyenera kufafaniza anthu oipa chotere mu dziko lino. Onse ayenera kuphedwa!”

Komabe, zoona zake ndi zakuti si dzigawenga zokha zankhanza zomwe zimakhala ndi khumbo lokupha mu mitima yao, koma ali yense padziko lino lapansi ali ndi khumbo lakupha mofanana. Ambuye akuti ali yense ali ndi khumbo lakupha mu mtima. Izi ndi zomwe ambuye akunena kwa ife pomwe anyang’ana mkati mwa mitima yathu, ndipo tiyenera kuvomereza ndi kuulula, “”ndine wochimwa wakupha.” Mulungu akunena kuti muli maganizo oipa komanso khumbo lakupha mumtima. Chocho tiyeni tonse tivomereze Mau a Mulungu. Pamene mbadwo umenewu ukutembenukira ku zoipa chotere, chili chonse chomwe munthu adzakhale nacho ngati chida chomtetezera chidzakhala chida chophera, osati mipeni, chabe komanso mifuti. Izi zili chonchi chifukwa cha kupha mu mtima mwa munthu. Anthu adzaphana okha okha pa kuyambana kwakung’ono. Komabe, ine ndikunena zimenezi kuti ndiunikire zimenezi mwa chilengedwe, tonse tili ndi khumbo lakupha mu mitima yathu.

Tiyenera kuzindikira apa kuti aliyense ndi oipa motere chifukwa aliyense anabadwa ndi khumbo loipa chotere. Si m’mene zilili kuti athu ena amabadwa oipa pamene ena ai. Koma, ali yense amabadwa wakupha komanso munthu oipa. Pamene Mulungu ananena kuti ali yense ndi oipa, ananena zimenezi chifuwa aliyense ndi oipadi. Palibe ali yense amene ali wabwino. Chikhulupiliro choyenera chikufunika ife tonse kuzindikira Mau a Mulunguwa ndi kuvomereza kwa iwo. Ndi chifukwa chakuti anthu ali ndi khumbo loipa ndi pomwe iwo amachita zoipazo ndi machitidwe awo.Khumbo Lonyansa Mwa Munthu


Mulungu akunenanso kuti munthu ali ndi khumbo lonyansa mkati mwake, koma mukugwirizananazo zimenezo? Kodi mukuvomereza kuti muli ndi khumbo lonyansa mkati mwanu? Ali yense ali khumbo la zilakolako mu mtima. N’chifukwa chake mafakitole a zolaula ayambukila kwambiri m’dziko muno.munthu angapeze ndalama mosavuta mu kuchita zolaula. Ngakhale pamene mitundu ina ya malonda ikubwerera m’mbuyo, koma malonda azolaula imachitabe bwino, ichi ndi chifukwa chakuti mkati mwa mtima wa ali yense muli zilakolako.Chibadwidwe cha Uchimo cha Munthu Chimabala Zipatso za Uchimo 


Mtengo wa ma apo umabala ma apo, mtengo wa mapeyala umabala mapeyala mtengo wa madeti umabala madeti, komanso mtengo wa pesimoni umabala ma pesimoni. Chimodzi modzinso, chifukwa ife tonse tinabadwa ndi mitundu khumi ndi iwiri ya uchimo mu mitima yathu, tonse a ife timachita tchimo mu myoyo yathu. Izi ndi zomwe Ambuye ananena. Kodi mukubvomereza zomwe Ambuye ananena apa kwa ife, kuti chomwe chimachoka mu mtima mwa munthu ndi chomwe chimaipitsa munthu? Ngati tagwirizana ndi Mau amenewa a Mulungu, ndiye kuti sitingakwanitse koma kubvomereza kuti, “inde, Ambuye. Tonse ife indedi ndi oipa ana a njoka akuchita zoipa. Mukunena zoona.” Ndipo ife tiyenera kubvomereza zimenezi. Tiyenera kubvomereza tokha ndi kuzindikira Mau a Mulungu. Monga Yesu Kristu anadzipereka yekha ku chifuniro cha Mulungu, choncho ifenso anthu tiyenera kuzindikira Mau a Mulungu mwakuzipereka. Pokhapo ndipamene ife tingapulumutsidwe ku machimo athu onse kudzera mu Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu operekedwa ndi Mulungu.

Korea ndi malo akulu okhala ndi nyengo zinayi za padera. Koma nyengo zimasintha osati mu Korea mokha, koma dziko lonse lapansi, monga m’mene nyengo ili yonse imabwera mu nthawi yake, choncho ndi m’menenso mitundu khumi ndi iwiri ya uchimo mu mitima yathu imachitira, kutipanga ife kuchimwa. Kungakhale kupha tsiku la lero, chilako lako mawa, maganizo oipa tsiku lotsatira, chinyengo tsiku linali, kuba tsiku lotsatira lake, kupusa tsiku linalo komanso kunyoza Mulungu tsiku lotsatiralo-machimo onse amene ife timachimwa tsiku ndi tsiku la mwezi uli onse la chaka chili chonse ndi osatha. Tsiku silitha osachita tchimo lili lonse. Ndi chifukwa chake ife tiri mazira a tchimo omwe sitingadzithandize koma kupiliza kuchimwa kupatula kuti ife tokha sitifuna kuchita tchimo kachiwiri.

Tiyeni tione mtengo wa ma apo. Kodi mtengo uli onse wa ma apo subala ma apo chifukwa iwo sufuna kubala? Chifukwa choti mtengo wa ma apo waganiza, “sindikufuna kubala apo ili yonse,” kodi iwo subala apo ili yonse? Ai, nzosatheka. Ndi dongosolo la chilengedwe kuti mtengo wa apo upange maluwa, ubale ma apo muchilimwe, kupsa ndi kugwa nthawi yokolola. Chimodzi modzi ndi m’mene ziliri kuti ali yense amachimwa moyo wake onse.Chitetezero Cha Machimo Chapangidwa Mwa Ubatizo Wa Yesu Ndi Mwazi Wake Pamtanda


Tiyeni tibwerere ku Mau kuti tione onse awa ochimwa, amene ali ana a njoka akuchita zoipa, m’mene angalandilire chikhululukiro cha machimo kwa Mulungu ndi kupanga chitetezero cha machimo ao onse kukhala muchimwemwe. Ndikupemphani inu kumvetsera Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo mwacheru apa ndikupeza mayankho ku funsoli. 

Tikabwerera ku Chipangano Chakale, kunalembedwa mu Levitiko 4:27-31: “Ndipo akacimwa wina wa anthu a m’dziko, osati dala, pa cina ca zinthu ziri zonse aziletsa Yehova, naparamula; akamdziwitsa kucimwa kwace adacimwako, azidza naco copereka cace mbuzi yaikazi, yopanda cirema, cifukwa ca kucimwa kwace adakucita. Aike dzanja lace pamutu pa nsembe yaucimo, naiphe nsembe yaucimo pamalo pa nsembe yopsereza. Ndipo wansembe atengeko mwazi ndi cala cace, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wonse patsinde pa guwa la nsembe. Nacotse mafuta ace onse, monga umo amacotsera mafuta pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo awatenthe pa guwa la nsembe akhale pfungo lokoma la kwa Yehova; ndi wansembe amcitire comtetezera, ndipo adzakhululukidwa.” 

Mu nthawi ya Chipangano Chakale, pamene a Israyeli anachimwira Mulungu, kodi iwo onse analandira bwanji chikhululukiro cha machimo awo? Baibulo likunena kuti mu nthawi ya Chipangano Chakale pamene munthu wachita tchimo, munthuyu ankapeza chikhululukiro cha machimo ake mwakupatsira machimowo ku nyama ya nsembe mwa kuika manja ake pamutu pake. Kunalembedwa mu Levitiko 1:2-4: “lankhula ndi ana a Israyeli, nunene nao, ali yense mwa inu akabwera naco copereka ca kwa Yehova, muzibwera naco copereka canu cikhala ca zoweta, ca ng’ombe, kapena ca nkhosa, kapena ca mbuzi. Copereka cace cikakhala nsembe yopsereza ya ng’ombe, azibwera nayo yaimuna yopanda cirema; abwere nayo ku khomo la cihema cokomanako, kuti alandirike pamaso pa Yehova. Ndipo aike dzanja lace pamutu pa nsembe yopsereza; ndipo idzalandiridwa m’malo mwace, imtetezere.” 

Mulungu anakonza nyama za nsembe zapadera za anthu a Israyeli kuti achotsere iye machimo ao onse. Ndipo kwalembedwa apa, “Ndipo aike dzanja lace pamutu pa nsembe yopsereza.” Mu Chipangano Chakale, kuika dzanja la munthu pa nyama yansembe kukutanthauza kupereka machimo ake pa nyama. Choncho tsopano, pamene munthu watsegula chipata cha bwalo la chihema ndi kulowa mkati, chinthu choyambilira chomwe iye ankaona chinali guwa la nsembe lopsereza, ndipo guwali linali lopangidwa monga bokosi lokulilapo kuposa guwa lili panoli, linali ndi nyanga mu ngodya zonse zinayi. Apa ndipamene a Israyeli ankaperekera nsembe zao ndipo motero kupereka machimo ao, komanso kupha nyama.

Mulungu anati mu Levitiko, “Ndipo aike dzanja lace pamutu pa nsembe yopsereza; ndipo idzalandiridwa m’malo mwace, imtetezere.” Pamene mu Israyeli waika manja ake pamutu pa nyama yansembe, machimo ake ankaperekedwa pa nyamayo, ndipo atapatsila machimo pa nyamayo podzera kuika manja ake, nyamayi ankalandira machimo ake ndi kupanga chitetezero m’malo mwake. Ochimwa kenako ankadula khosi la nyamayo ndi kuchotsa mwazi wake. Wansembe kenako, ankaika mwazi wa nyamayo pa nyanga za guwa la nsembe, kudula nyamayo muzidutswa, kuika nyamayo pa guwa, kutaya zonse zoipa zamkati komanso zipwiza, ndikutentha nyamayo ndi moto kupereka pfungo lokoma kwa Mulungu. Umu ndi m’mene a Israyeli ankapezera chikhululukiro cha machimo ao onse. Iyi inali nsembe yomwe anthu a Israyeli ankachotseredwa machimo ao tsiku ndi tsiku.

Kuonjezerapo, anthu a Israyeli anali ndi mwambo wina wa nsembe omwe unkalola iwo kupanga chitetezero cha machimo ao a chaka chonse, ndipo nsembe ya tsiku la chitetezero cha machimoyi inali ndizochitika zambiri kusiyana ndi nsembe ya masiku onse. Choyambilira, pamene panali ochimwa m’modzi amene ankapatsira machimo ake ku nyama yopanda chilema pamene chitetezero chinkachitika kumachmo ake a tsiku ndi tsiku, pa nsembe ya chaka ya tsiku la chitetezero, anali mkulu wansembe amene ankaika manja ake pa nyama ya nsembe m’malo mwa anthu onse a Israyeli ndikupatsira machimo ao panyama pamene iwo ankayang’anira. Kusiyana kwina ndi kwakuti mkulu wa nsembe ankatenga mwazi wa nyama kupita nao m’malo opatulika ndi kuwaza mwaziwo kasanu ndi kawiri pa mpando wachifundo kum’mawa. Munjira imeneyi, patsiku la khumi la mwezi wa chisanu ndi chiwiri, mkulu wansembe ankapanga chitetezere cha machimo onse a chaka a anthu a Israyeli (Levitiko 16:5-27).

Choncho tsopano, tiyenera kusuntha kumvera kwathu ndi kufufuza m’mene ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe ya Chipangano Chakale inakwanitsidwira m’Chipangano Chatsopano, komanso m’mene lemba la Mulungu losatha lasungidwira ndi kupitilira popanda kusintha.

Kodi n’chifukwa chiani Yesu anayenera kufa pamtanda? Kodi ndi chiani choipa chimene Mulungu anachita pa dziko lino kuti Iye apachikidwe mpaka kufa? Ndani amene anakakamiza Yesu Krisyu kuti afe pamtanda? Pamene ochimwa onse a dziko lino anagwa mu uchimo-izi zikutanthauza inu ndi ine-Yesu Kristu anadza pa dziko lino kupulumutsa ochimwa amenewu, ana a njoka ochita zoipa, ku chiweruzo chonse cha uchimo. Kenako, Iye anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi mu mtsinje wa Yordano kuti apange chitetezero cha machimo anu ndi yanga, ndipo m’malo mwathu Iye anasenza chilango cha uchimo chomwe ife tonse tinkayenera kusenza mwa ife tokha. Kunena kuti Yesu anabatizidwa ndi kukhetsa mwazi Wake pamtanda ndi chimodzi modzi mwambo wa nsembe ya Chipangano Chakale ya nsembe yauchimo, pomwe manja ankaikidwa pamutu pa nyama ya nsembe kuti iphedwe pa guwa la nsembe. 

 Mu nthawi ya Chipangano Chakale, a Israyeli ankaika manja ao pamutu pa nyama ya nsembe ndikuulula machimo ao, ndipo kuti achotseredwe machimo ao onse, iwo ankadula khosi la nyama yomwe apatsirapo machimo ao, kuchotsa mwazi wake, ndi kupereka nsembeyi kwa Mulungu kuti apange chitetezero cha machimo ao. Chimodzi modzinso, Yesu Kristu nayenso anapereka nsembe yofanana ya chitetezero cha machimo. Iye anabatizidwa ndi kukhetsa mwazi Wake pamtanda mpaka kufa pofuna kuti Mulungu afufute machimo anu onse ndi anga, ndikupulumutsa ife ku machimo athu onse.

Sikulakwitsa kunena kuti inu ndi ine ndife okhudzidwa pa imfa ya Yesu Kristu. Ganizani zomwe zinachitika mu nyama za nsembe zopanda chilema za m’Chipangano Chakale. Kodi nyamazi zinkadziwa kuti tchimo ndi chiani? Ai, sizinkadziwa; palibe nyama yomwe inkadziwa tchimo. Koma a Israyeli ankaika manja ao pamutu pa nyamazi ndi kupereka machimo ao pa izo. Momveka bwino, payenera kukhalanso m’chitidwe ofanana momwe Yesu angalandilire machimo onse a mtundu wa anthu pa thupi lake.

Kulankhula mwachidule, Yesu Kristu anali Mwana wa Mulungu opanda uchimo, ndipo Iye sanachimwepo tchimo lili lonse. Koma kuti asenze machimo onse a mtundu wa anthu ndi a dziko lapansi, Iye anabatizidwa mu mtsinje wa Yordano pa dzaka makumi atatu, ndipo izi zinachitika kuti apange chitetezero cha machimo onse a mtundu onse wa anthu. Chinali chifukwa cha kuti Yesu analandira machimo athu onse mu mtsinje wa Yordano pomwe Iye anapachikidwa ndi kufa. Utumiki onsewu unali ntchito ya chipulumutso yochitika kuti afufute machimo a ali yense ochimwa. Zimenezi zinalembedwa mu Mateyu 3.Chiyambi Cha Uthenga Wabwino Wa Chitetezero Cha Machimo


Tiyeni tsopano tibwerere ku Mateyu 3:13-16 “Pamenepo Yesu anacokera ku Galileya nadza ku Yordano kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye. Koma Yohane anati amkanize, nanena, Ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi? Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero. Pamenepo anamlola Iye. Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anaturuka m’madzi.” 

Ndizofunika kotheratu kwa ife tonse kumvetsetsa chifukwa chimene Yesu anabatizidwira pa dzaka makumi atatu. Kunali kucotsa machimo onse a anthu ndi kukwaniritsa chilungamo chonse cha Mulungu kuti Iye anabatizidwa. Pofuna kupulumutsa anthu onse kumachimo ao, Yesu opanda chilema payekha anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Ndipo pochita izi, Iye anasenza machimo onse a dziko lino, kuchotseratu onse, ndi kupulumutsa anthu onse. Kuti tilandire chikhululukiro cha machimo, tiyenera kukhulupilira mu choonadichi. Ntchito ili pa ife kukhulupilira mu choonadichi.

Kodi ubatizo wa Yesu ukutanthauza chiani? Tanthauzo lake ndi chimodzi modzi ndi lakuika manja m’Chipangano Chakale. M’Chipangano Chakale, inali nyama ya nsembe yomwe inkasenza machimo a Israyeli kudzera mukuika manja kapena a ochimwa kapena manja a mkulu wansembe, koma m’Chipangano Chatsopano, pamene Yesu Kristu Mwini anadza mu dziko lino kudzapulumutsa ife, Iye payekha analandira ndi kusenza machimo athu onse kudzera mu kuika manja a Yohane Mbatizi. Pa nthawiyo, Mulungu Atate anadzutsa Yohane Mbatizi kuti akhale m’modzi woimilira wa anthu onse, ndipo Iye analola iye kubatiza Yesu m’malo mwa munthu ali Yense. Kukamba mwa uzimu, Mau oti, “ubatizo” akutanthauza “kupatsira pa, kusamutsa, kukwirira, kapena kutsuka” ndipo matanthauzo onsewa akuchokeranso mu “kuika manja.”

Choncho tsopano, kodi mukuzindikira chifukwa chimene Yesu Kristu anayenera kulandira ubatizo Wake wa chitetezero cha machimo kwa Yohane Mbatizi pamene Iye anadza pa dziko lino? Kodi mukukhulupilira mwa Yesu ndi kumvetsetsa kumeneku? Yesu anabatizidwa kuti anyamule machimo onse a dziko pa thupi Lake, tchimo lili lonse lomwe inu ndi ine komanso mtundu onse wa anthu timachita ndi matupi athu ndi mitima mpaka tsiku la kufa monga ana a njoka ochita zoipa. Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi kuti akwaniritse Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo.

Kunanenedwa mu Mateyu 3:15, “pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero.” Kukwaniritsa chilungamo chonse apa kukutanthauza kupanga munthu ali yense opanda uchimo ndikumasula ali yense ku machimo onse a dziko. Mwanjira ina, Yesu Kristu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi chifukwa cha ochimwa onse. Monga kwaonetsedwa mu Mateyu 3:13-17, pamene Yesu Kristu anabatizidwa mu mtsinje wa Yordano, machimo onse a anthu anaperekedwa pa Iye. Ndipo pamene anasenza machimo onse a munthu ali yense pa nthawiyo, Yesu Kristu anafa pamtanda dzaka zitatu zotsatira zake, ndipo Iye anauka kwa akufa m’masiku atatu. Kuti achotse machimo onse a dziko lino, Iye anabatizidwa kamodzi, kufa pamtanda kamodzi, ndi kuuka kwa akufa kamodzi. Kwa iwo one amene akufunitsitsa kulandira chikhululukiro cha machimo kwa Mulungu, kwa onse a okhulupilira Ake, Yesu wabweretsa chipulumutso kamodzi kokha. 

Yesu anayenera kubvala kolona wa minga, kuweruzidwa pa bwalo la Pilato ndi kupachikidwa monga wachifwamba ndi kukhetsa mwazi Wake onse mpaka kufa. Kodi n’chifukwa chiani nanga Yesu anayenera kuzunzika chotere? Chifukwa chakuti Iye ananyamula machimo onse a anthu pa dziko lino kudzera mu ubatizo Wake, chifukwa chakuti Iye anatenga machimo anu onse ndi anga, Yesu anayenera kufa pamtanda motere.

Ife tonse tiyenera kukhulupilira mu Mau a chipulumutso ndi kuyamika Mulungu potipulumutsa ife mu njira imeneyi. Yesu sakanapulumutsa ife ku machimo onse a dziko mwanjira ina koma mwanjira imeneyi yokha-ndiye kuti, mwa kubatizidwa, kupachikidwa komanso kuuka. Pamene Yesu Kristu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi kuti alandire machimo onse a dziko, Iye anachotsa machimo onse, Iye anapulumutsa ife ku machimo onse a dziko ndipo Iye wapulumutsa okhulupilira Ake onse. Anthu ena angaganize kuti “kodi Yesu sanachotse tchimo lathu lobadwa nalo lokha?” koma awa ndi maganizo ao chabe; Mulungu analemba momveka bwino mu Baibulo kuti Yohane Mbatizi anapereka machimo onse a dziko kwa Yesu pamene iye anambatiza Iye, pomwe Yesu ananyamula machimo onse ndipo kuti Yesu anafufuta machimo onse a anthu. Yesu Mwini ananena mu Mateyu 3:15, “Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero.” Kunena kuti Ambuye anakwaniritsa chilungamo chonse kukutanthauza kuti Iye anafufuta machimo onse a dziko. 

Kodi Yesu anachotsa machimo a ali yense amasiku onse mu dziko lino? Iye indedi anachotsa onse. Kuti tipeze chitsimikizo cha izi, tiyeni tibwerere ku Chipangano Chakale ndi kuona nsembe ya tsiku la chitetezero komanso ntchito ya mkulu wansembe monga afotokozera mu Levitiko 6.Nsembe Yomwe Inkatetezera Machimo Onse a Chaka a Anthu Onse a Israyeli


Kwalembedwa mu Levitiko 16:6-10, “Ndipo Aroni abwere nayo ng’ombe ya nsembe ya ucimo, ndiyo yace yace, nacite codzitetezera iye yekha, ndi mbumba yace. Ndipo atenge mbuzi ziwirizo naziimike pamaso pa Yehova pa khomo pa cihema cokomanako. Ndipo Aroni ayese maere pa mbuzi ziwirizo; maere amodzi kwa Yehova, ndi amodzi kwa Azazeli ndipo Aroni abwere nayo mbuzi imene adaigwera maere a Yehova, naiyese nsembe ya ucimo. Koma mbuzi imene adaigwera maere a Azazeli, aiike yamoyo pamaso pa Yehova, kuti acite nayo cotetezera, kuitumiza kucipululu ikhale ya Azazeli.” Apa Baibulo likufotokoza m’mene Aroni ankaperekera ng’ombe yamphongo monga nsembe yake yauchimo ndikutenga mbuzi ziwiri kupereka izo kwa Mulungu pakhomo la chihema chokomanako. Kwalembedwa apa kuti, “Ndipo Aroni ayese maere pa mbuzi ziwirizo; maere amodzi kwa Yehova, ndi amodzi kwa Azazeli.” Kuti apulumutse anthu a Israyeli, Aroni ankafunika mbuzi yamoyo. 

Malingana ndi ndondomeko yakaperekedwe ka nsembe yokhazikitsidwa ndi Mulungu ya Chipangano Chakale, munthu akapatsira machimo ake a tsiku ndi tsiku kunyama yansembe poika manja ake pamutu pa nsembe payekha, koma machimo a chaka chonse a anthu a Israyeli ankhaperekedwa ndi mkulu wansembe m’malo mwao pa tsiku la khumi la mwezi wa chisanu ndi chiwiri. Kwalembedwa mu Levitiko 16:29-31, “Ndipo lizikhala kwa inu lemba losatha; mwezi wacisanu ndi ciwiri, tsiku lakhumi la mweziwo, muzidzicepetsa, osagwira nchito konse, kapena wa m’dziko, kapena mlendo wakukhala pakati panu; popeza tsikuli adzacitira inu cotetezera, kukuyeretsani; adzakuyeretsani, kukucotserani zoipa zanu zonse pamaso pa Yehova. Likhale kwa inu sabata lakupumula, mudzicepetse; ndilo lemba losatha.” Pamene anthu a Israyeli ankabweretsa nsembe zao za masiku onse kuchihema, iwo ankaulula machimo ao ndi kupereka machimowo pa nsembezo mwakuika manja ao pamutu pake, kudula khosi lake ndi kuchotsa mwazi wake, kenako kupereka mwaziwo kwa wansembe. Ikalandira machimowa mwakuika manja, nyamayi kenako inkaphedwa kuti ichotse machimo onse. Mulungu kenako ankalandira nsembeyo m’malo mofuna imfa ya a Israyeli. Nyama zoyera zosankhidwa ndi Mulungu, monga anaankhosa, mbuzi, anaang’ombe, komanso ng’ombe za mphongo, zinkalandiridwa monga zopereka za nsembe, ndipo Mulungu ankalandira nsembe ili yonse yomwe inkaperekedwa mwa malamulo Ake.

Chifukwa Mulungu ndi wachifundo, Iye anafuna kupulumutsa anthu onse a Israyeli, ndipo Iye anabvomera ochimwa kupereka machimo ao kwa nyama yansembe ndi kulola nyamayi kuphedwa m’malo mwao. Motere, ndondomeko yakaperekedwe ka nsembe ya Chipangano Chakale inabweretsa chikhululukiro cha machimo kwa a Israyeli pamene iwo ankapereka machimo ao ku mwanawankhosa kapena mbuzi mwakuika manja ao pamutu ake, kupha nyamayi ndi kuchotsa mwazi wake, ndi kupereka mwaziwo kwa wansembe. 

Ngakhale anthu a Israyeli anayenera kupeza chikhululukiro cha machimo ao a tsiku ndi tsiku mu njira imeneyi, kunali kosatheka kwa iwo kupereka nsembe zambiri masiku onse. Choncho pa tsiku la khumi la mwezi wachisanu ndi chiwiri, mkulu wansembe ankaika manja ake pamutu pa mbuzi yamoyo m’malo mwa anthu onse a Israyeli, kupereka machimo ao onse a chaka ku nsembe ya nyamayi kamodzi kokha. Kodi cheni cheni chomwe mkulu wansembe ankachita chinali chiani? Choyamba, Aroni ankaika manja ake pamutu pa mbuzi ndi kuulula machimo onse a Israyeli omwe iwo anachita chaka chonse, kunena kuti “anthu a Israyeli apha, achita chigololo, komanso kuba. Akhala a nsanje, akangana okha okha, aperekera umboni wabodza.” Iye kenako ankadula khosi la nyama ya nsembeyo, kuchotsa mwazi wake, kupereka mwaziwo m’malo opatulika mwa iye yekha, ndi kuwaza mwaziwo kasanu ndi kawiri m’menemo. Nambala ya chisanu ndi chiwiri mu Baibulo imatanthauza ungwiro. Chinthu choyamba chomwe mkulu wansembe ankachita chinali kupereka machimo onse a chaka a anthu onse a Israyeli kunyama ya nsembe, ndipo zikatha izi nyamayo inkaperekedwa ndi kuphedwa m’malo mwao. 

Chifukwa Mulungu ndi wa chilungamo, pofuna kupulumutsa anthu a Israyeli ku machimo ao onse a kuthupi, Iye anayenera kupereka nsembe m’malo mwao. Iye anachita zimenezi chifukwa Iye ndi wachifundo. Choncho, pamene mkulu wansembe ankawaza mwazi wansembe kasanu ndi kawiri pampando wachifundo kum’mawa, machimo onse a anthu onse a Israyeli anatsukidwa pa tsiku limodzi, patsiku la khumi la mwezi wachisanu ndi chiwiri.

Chaka chili chonse, pa tsiku la khumi la mwezi wa chisanu ndi chiwiri, anthu a Israyeli ankapereka nsembe pa tsiku la chitetezero cha machimo, ndipo pa tsikuli mbuzi ziwiri zinkaperekedwa. Imodzi mwa iyo ndi “mbuzi yamoyo” zomwe zikutanthauza, “kumasulidwa,” ndipo mbuzi yamoyoyi ya Chipangano Chakale ndi chithunzi thunzi cha Yesu Kristu m’Chipangano Chatsopano. Monga Baibulo likunena, “Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wace wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha” (Yohane 3:16).

Izi zikutanthauza kuti Mulungu anaptsa ife Mwana Wake kuti akhale Mwana wathu wakhosa wansembe. Mwanjira ina, Yesu anadza kwa ife monga Mpulumutsi amene anasenza machimo onse a dziko mwa kubatizidwa ndi Yohane Mbatizi ndi kupulumutsa ife ku machimo onse. Ndi chifukwa chake Iye akutchedwa Mesiya yemwe ndi Mpulumutsi. Choncho, dzina loti “Yesu Kristu” likutanthauza Mfumu ya mafumu onse amene anadza kupulumutsa ochimwa onse. Kunena kwina, monga anthu onse a Israyeli ankachotseredwa machimo ao onse a chaka chonse pa tsiku la chitetezero m’Chipangano Chakale, m’Chipangano Chatsopano, Yesu Kristu anadza pa dziko lino lapansi dzaka 2000 zapitazo, anabatizidwa kunyamula machimo onse a anthu, ndi kupanga chitetezero cha tchimo lili lonse mwa kukhetsa mwazi Wake pamtanda.

Tiyeni tiwerenge mu Levitiko 16:21-22, “Ndipo Aroni aike manja ace onse awiri pamutu pa mbuzi yamoyo, ndi kubvomereza pa iyo mphulupulu zonse za ana a Israyeli, ndi zolakwa zao zonse, monga mwa zocimwa zao zonse; naike izi pamutu pa mbuziyo, ndi kuitumiza kucipululu ndi dzanja la munthu wompangiratu, ndi mbuziyo isenze yokha mphulupulu zonsezo kumka nazo ku dziko la pa lokha; ndipo azitaya mbuziyo m’cipululu.” 

Monga kwalembedwa mu Levitko 1, ndimeyi ikupanganso kumvetsetsa kuti machimo a Israyeli anaperekedwa pa nyama yansembe kudzera mukuika manja a Aroni. Pamene Baibulo linakamba za “mphulupulu zonse za ana a Israyeli” apa mu Levitiko 16:21, mphulupulu zikutanthauza machimo onse a Israyeli ochitidwa ndi mitima yao kapena machitidwe ao, ndipo mkulu wansembe ankapereka mphulupulu zao zonsezi pa mbuzi yamoyo mwakuika manja ake pamutu pake. Kuchokera Ku Lamulo, Muyenera Kuzindikira Zotsatira Zonse Za Machimo Anu


Lamulo la Mulungu muli ndime zokwanira 613 komanso malamulo. Mu zoona zake, komabe, tonse talephera kuchita zomwe Mulungu anatiuza ife kuti tichite ndipo tachita zomwe Iye anatiuza kuti ife tisachite. Choncho tonse ndife ochimwa. Baibulo linalemba kuti Mulungu anatipatsa ife Lamulo kuti tizindikire machimo athu (Aroma 3:20), ndipo izi zikutanthauza kuti Mulungu anatipatsa ife Lamulo kutiphunzitsa ife kuti ndife ochimwa. Mwanjira ina, lamulo silinapatsidwe kwa ife patsogolo pakuti ife ndi okhonza kulemekeza malamulo onse, ndipo choncho tiyenera kusunga, koma m’malo mwake, linapatsidwa kwa ife kuti tizindikire machimo athu. Mulungu sanapatse ife Lamulo kuti tisunge lemba lili lonse mwa ngwiro, ngati kuti izi zinali zotheka kwa ife. Kusunga lamulo lonse ndikupitilira umunthu wathu; ndi chimodzi modzi kuyembekezera chilombo kukhala monga munthu. Choncho cholinga cha lamulo chinali kutipanga ife kuzindikira machimo athu, osati kulemekeza Lamulolo mwa ngwiro. 

Kunena kwina, Mulungu anapatsa ife Lamulo chifukwa ngakhale ife tinali ochimwa otheratu, sitinazidziwe tokha. Mwa Lamulo Mulungu akunena kwa ife, “ndinu akupha komanso achigololo, ndipo maganizo anu nthawi zonse ndi oipa.” Mulungu anauza ali yense osapha, koma ndi mwachilengedwe chao kuti anthu adzipha mu mitima yao komanso nthawi zina ngakhale kuphadi m’machitidwe. Choncho tsopano, pamene munthu wachita zomwe Mulungu anamletsa kuti asachite kudzera mwa Lamulo, iye amazindikira kuti iye achita cholakwika, kuti iye wachita tchimo, ndipo chotero kuti iye ndi ochimwa. Mwanjira ina, ndi pamene timachita china chake choletsedwa pomwe timazindikira kuti ndife ochimwa. 

Choncho m’Chipangano Chakale, kupulumutsa anthu onse a Israyeli ku machimo ao Mulungu analola Aroni kutumikira nsembe ya tsiku la chitetezero cha machimo, ndipo ponyamula udindo umenewu ndi kukwaniritsa unsembewu, Aroni anapanga kuthekera kwa a Israyeli onse kupanga chitetezero cha machimo ao a chaka. Monga kwanenedwa, panali nyama ziwiri za nsembe zoperekedwa pa tsiku la chitetezero cha machimo, ndipo imodzi mwa iwo inkaperekedwa kwa Mulungu muchihema pamene Aroni anapatsira machimo onse a Israyeli paiyo mwakuika manja ake, pamene mbuzi inayo inkamasulidwa yamoyo mchipululu. Aroni ankaikanso manja ake pamutu pa mbuzi yachiwiriyo ndi kupatsira machimo a Israyeli, koma iye ankachita zimenezi pamene iwo ankayang’anira. Ndi manja ake pamutu pa mbuzi, Aroni anaulula machimo onse a Israyeli a chaka chonse, ndipo kenako ankapereka mbuzi yamoyoyi kwa munthu ompangiratu kuti aitumize kuchipululu.

Mnzinda wa Palestina ndi chipululu, ndipo mbuzi yamoyoyi inkatsogololedwa m’chipululu chopanda malire chotere ndikusiidwa kumeneku. Pamene anthu a Israyeli aona mbuziyi ikunyamula machimo a chaka chonse kupita nao m’chipululu, iwo anadziwa kuti machimo ao atha ndipo apeza mpumulo mu mitima yao, pamene mbuzi yamoyo pamapeto pake inkaonongeka pena pake m’chipululu. Itatopa kuzungulira m’chipululu koma mbuziyo inkaonongeka itanyamula machimo a chaka a anthu a Israyeli, ndipo ndi imfayi inkachita chitetezero cha machimo onse.

Tsopano, Mulungu akunena kwa ife kuti Yesu ndi mbuzi yathu yamoyo, ndipo kuti kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, Mulungu Mwini anachotsa machimo onse masiku onse ndi macimo onse a moyo wathu onse. Yesu ndi Mulungu Mwini ndi Mpulumutsi wathu. Iye ndi Mwana wa Mulungu amene anadza kupulumutsa ife ku machimo onse a dziko, ndipo Iye ndi Mlengi amene anapanga ife. Pamene anadza kupulumutsa ife ku machimo onse a dziko omwe timachita mu thupi lathu, Yesu anayenera kubatizidwa ndi Yohane Mbatizi kupanga chitetezero osati cha machimo a masiku onse omwe timachita koma machimo onse amene sitinachitepo mu dziko lino, ngakhale mu mitima yathu kapena ndi thupi lathu, ndikukwaniritsa chilungamo chonse cha Mulungu.

Dzaka zitatu asanafe pamtanda, pamene Yesu Kristu anayamba utumiki Wake woonekera pa dziko lino pamene anafika dzaka makumi atatu, chinthu choyambilira chomwe Iye anachita chinali kulandira machimo onse a dziko mu mtsinje wa Yordano kudzera mwa Yohane Mbatizi, ndipo kunali kuchokera pa nthawi imeneyi pomwe Ambuye anayamba kugwira ntchito pofuna kutsiriza chipulumutso cha anthu onse komanso chikhululukiro cha machimo ao.

Ndi madzi olekeza mchiuno mu mtsinje wa Yordano, Yohane Mbatizi anabatiza Yesu mwa kuika manja ake pamutu pake ndi ku m’miza Iye m’madzi. Ubatizowu apa ukutanthauza kuika manja kwa m’Chipangano Chakale, ndipo iyi ndi njira yomwe Yesu analandira machimo onse a anthu. Ndipo kuti Yesu anamira m’madzi zikutanthauza imfa Yake, ndipo kuturuka kwake m’madzi kukutanthauza kuuka Kwake. Mwakulandira ubatizo kwa Yohane Mbatizi, Yesu Kristu anaika maziko oyenera kuti akwaniritse chilungamo chonse kudzera mu ntchito zitatu zimenezi. 

Tapulumutsidwa pokha pokha ngati tadzipereka ku Mau a Mulungu omwe Yesu anatipulumutsira ife. Mulungu anasankha kupulumutsa ife kudzera mwa Yesu Kristu mu njira imeneyi, ndipo Iye wakwaniritsa chipulumutso chathu m’Chipangano Chatsopano malingana ndi Mau a pangano Lake olonjezedwa m’Chipangano Chakale. Ndipo Yesu Kristu anasenza machimo onse a dziko ndi kunyamula iwo kupita nao pamtanda.

Kwalembedwa mu Yohane 1:29, “M’mawa mwace anaona Yesu alinkudza kwa Iye, nanena, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa cimo lace lapansi!” Yohane Mbatizi akuchitira umboni apa kuti Yesu Kristu anachotsa machimo onse a dziko. Machimo onse a anthu anaperekedwa pa Yesu Kristu pamene Iye anabatizidwa. Khulupilirani mu zimenezi! Kenako mudzalandiradi chitetezero cha machimo mwa chikhulupiliro. Tonse a ife tiyenera kukhulupilira mwachikhulupiliro mu Mau a Mulungu. Kuika pambali maganizo athu osamvera ndi malingaliro athu, tiyenera kudzikuthula ku Mau a Mulungu onena kuti Yes anatenga machimo onse a dziko, ndipo tiyenera kukhulupilira mu Mau amenewa popanda kukaikira.

Kuti Yesu anachotsa machimo onse a dziko lino kamodzi kokha kukutanthauza chimodzi modzi chikhululukiro cha machimo chimwe chakwaniritsa chilungamo Chonse cha Mulungu. Ndipo “kuika manja” komanso “ubatizo” apa ukutanthauza chinthu chimodzi. “chili chonse, zonse,” komanso “chinthu chonse” ndi mau osiyana koma matanthauzo ake ndi ofanana. Chomodzi modzinso kuika manja m’Chipangano Chakale kukufanana ndi ubatizo m’Chipangano Chatsopano, omwe Yesu analandira njira yakuika manja, ndipo ndi mwa ubatizowu wa Yesu kuti machimo athu onse anatsukidwa, Baibulo likunena kuti Yesu anabatizidwa ndi kuweruzidwa pamtanda m’malo mwathu kupanga chitetezero cha machimo athu, ndipo tapulumutsidwa pkhulupilira mu Uthenga Wabwinowu oyamba.

Kodi, tsopano, ndi machimo a dziko otani amene Yesu anachotsa? Baibulo likunena kuti machimo omwe tinabadwa nao kuchokera m’mimba mwa mayi athu komanso khumbo lonse la uchimo limene likupezeka mu mtima mwathu, monga maganizo oipa, kuba, nsanje, kuyambana, kudana, kudzikudza komanso kupusa, onse ndi machimo a dziko, monga machimo onse a masiku onse komanso mphulupulu zomwe sitinachite ndipo tidzachita chifukwa cha kufooka kwathu, ngakhale m’machitidwe athu kapena mu mitima yathu. Tchimo lili lonse, mwanjira ina ndi tchimo la dziko lapansi.

Kwalembedwa mu Aroma 6:23, “Pakuti mphotho yace ya ucimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” Baibulo likunenanso mu Ahebri 9:22, “wopanda kukhetsa mwazi kulibe kumasuka.” Momwe Mau a Mulungu akunenera apa, mphotho ya tchimo lili lonse iyenera kuperekedwa popanda kulephera. Koma Baibulo likutiuzanso kuti pamene Yesu Kristu anadza pa dziko lino kupulumutsa ife ku machimo athu onse, Iye analipira mphotho ya tchimo lili lonse kamodzi kokha ndi moyo Wake, motero kupanga chitetezero cha machimo onse a munthu ali yense mu dziko lino. Chikhululukiro cha machimo choncho chimalandiridwa mwa kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, komanso mwa kukhulupilira kuti Yesu Mwini ndi Mpulumutsi.Chitetezero Cha Machimo a Mawa


Tchimo lili lonse lomwe tachita komanso tidzachite mpaka pamapeto pa moyo wathu onse ndi machimo a dziko, posatengera kuti anachitidwa liti. Kuchokera dzulo, lero mpaka mawa, kuchokera kukwawa mpaka kumanda, machimo onse omwe sitinachite ali pamodzi ndi machimo a dziko, ndipo Baibulo ikunena kuti machimo onse amenewa anaperekedwa pa Yesu Kristu kudzera mu ubatizo Wake, ndipo Ambuye anachotsa machimo onse kwa Ife. Tchimo lili lonse lomwe ife tachita mpaka kufa laphatikizidwa mu machimo a dziko.

Tapulumutsidwa pokhapo ngati takhulupilira mu Uthenga Wabwino oyambawu wa Mulungu ndi kudzipereka tokha ku Mau Ake olembedwa, ndipo chikhululukiro cha machimo chikulandiridwa pokhapo ngati ife tachotsa maganizo athu osamvera. Komabe anthu ena angafunse mouma mtima “kodi Yesu angachotse bwanji machimo amene sitinachitepo?” ndikufuna ndifunse anthu otere mowabwezera, “kodi Yesu Kristu ayenera kudza kwa ife ndikukhetsa mwazi Wake kuti afufute machimo athu nthawi ili yonse imene tachita tchimo?”

Okondedwa okhulupilira anzanga, kubadwa mwatsopano, muyenera kutsata Lamulo la chitetezero cha machimo, pakuti Baibulo likunena kuti, “wopanda kukhetsa mwazi kulibe kumasuka” (Ahebri 9:22). M’Chipangano Chakale, kuti ali yense alandire chikhululukiro cha machimo, kunali kofunika kuti munthu ameneyo aike manja ake pamutu pa nyama yake ya nsembe kuti apatsire machimo ake pa iyo ndi kupha nyamayo. Pokhapo pamene mphotho yake ya machimo yaperekedwa ndi pamene iye ankapulumutsidwa. Ndi chimodzi modzinso pamene Mwana wa Mulungu anadza pa dziko lino kupulumutsa mtundu onse wa anthu ku uchimo; kuchotsa machimo athu onse, Iye anasenza machimo onse mwa kubatizidwa, anakhetsa mwazi Wake pamtanda, kuuka kwa akufa masiku atatu, ndi kukwera ku mwamba; ndipo Iye wakhala tsopano kudzanja la manja la mpando wa Mulungu Atate monga Mpulumutsi wathu wamuyaya.

Kuti tilandire chikhululukiro cha machimo, tiyenera kutaya malingaliro athu okhwima ndi kuika pambali maganizo a chipembedzo kuti chikhululukiro chathu cha machimo chibwere masiku onse a moyo wathu. Tiyenera kulandira chipulumutso chachikhululukiro cha machimo kamodzi kokha; sitingalandire chikhululukiro cha machimo masiku onse mwakupemphera mapemphero akulapa. Kudzera mu ubatizo wa Yesu, Mulungu Atate anapatsira machimo onse a dziko kwa Mwana Wake kamodzi kokha, ndipo atatha kuika machimo onsewa a dziko pa thupi la Mwana Wake, Mulungu Atate anapanga Iye kupachikidwa ndi kulangidwa m’malo mwathu, kuukitsa Iye kwa akufa, ndipo motero kuchotsa machimo athu onse.

Ambuye ananena mu Yesaya 53 kuti Iye anaika mphulupulu zathu pa Yesu, komanso mphulupulu ili yonse ya ali yense mu dziko lino, monga kwalembedwa: “Zoonadi Iye ananyamula zowawa zathu, ndi kusenza zisoni zathu: koma ife tinamuyesa wokhomedwa, wokanthidwa ndi Mulungu, ndi wobvutidwa. Koma Iye analasidwa cifukwa ca zolakwa zathu, natunduzidwa cifukwa ca mphulupulu zathu; cilango cotitengera ife mtendere cinamgwera Iye; ndipo ndi mikwingwirima yace ife tachilitsidwa. Tonse tasocera ngati nkhosa; tonse tayenda yense njira ya mwini yekha; ndipo Yehava anika pa Iye mphulupulu ya ife tonse” (Yesaya 53:4-6). 

Pena pake mu Chipangano Chatsopano, Aefeso 1:4 akuti, “monga anatisankha ife mwa Iye, lisanakhazikike dziko lapansi.” Mulungu akunena apa kuti Iye anatisankha ife mwa Kristu lisanakhazikike dziko lapansi kutipanga ife olungama ake komanso athu opanda chilema. Choncho, ife tiyenerakukhulupilira mu Mau ake olankhulidwa a madzi, mwazi, ndi Mzimu, komanso kudzipereka tokha ku Mauwo posatengera maganizo athu.

Mulungu akunena kwa ife apa kuti, Yesu Kristu Mwana wake wa nkhosa, anachotsa machimo onse adziko lapansi ndi kufafaniza onse, ndipo izi ndi zomwe zinachitika. Ahebri 10:1 akunena kuti, “Pakuti cilamulo, pokhala nao mthuzi wa zokoma zirinkudza, osati cifaniziro ceni ceni ca zinthuzo, sicikhozatu, ndi nsembe zomwezi caka ndi caka, zimene azipereka kosalekeza, kuwayesera angwiro iwo akuyandikira.” Izi zikutanthauza kuti kuika manja athu pa mwanawankhosa kapena ng’ombe yamphongo ndi kupereka tsiku ndi tsiku ngati nsembe sizingatipange ife angwiro. Popeza lamulo ndi mthunzi wa zokoma zirinkudza, si langwiro palokha, ndipo motero Mesiya alinkudza, Yesu Kristu Mwini wake, anasenza machimo onse a dziko lapansi kamodzi kokha kudzera mu ubatizio Wake omwe analandira kwa Yohane Mbatizi, monga m’mene mkulu wansembe ankaperekera machimo achaka chonse a anthu a Israyeli kamodzi kokha. Ndipo Ambuye indedi anachotsa machimo onse a dziko lapansi mwa kubatizidwa ndi kupachikidwa.

N’chifukwa chake Baibulo likunena mu Ahebri 10:9-18: “pamenepo anati, Taonani, ndafika kudzacita cifuniro canu. Acotsa coyambaco, kuti akaike caciwirico. Ndi cifuniro cimeneco tayeretsedwa mwa copereka ca thupi la Yesu Kristu, kamodzi, kwatha. Ndipotu wansembe ali yense amaima tsiku ndi tsiku, naturukira, napereka nsembe zomwezi kawiri kawiri, zimene sizikhoza konse kucotsa macimo; koma Iye, m’mene adapereka nsembe imodzi nsembe imozi cifukwa ca macimo, anakhala pa dzanja lamanja la Mulungu cikhalire; kuyambira pomwepo alindirira, kufikira adani ace aikidwa akhale mpando ku mapazi ace. Pakuti ndi cipereko cimodzi anawayesera angwiro cikhalire iwo oyeretsedwa. Koma Mzimu Woyeranso acitira umboni; pakuti adatha kunena: Ici ndi cipangano ndidzapangana nao, atapita masiku ajawo, ananena Ambuye: Ndidzapereka malamulo anga akhale pamtima pao; ndipo pa nzeru zao ndidzawalemba; ndipo macimo ao ndi masayeruziko ao sindidzawakumbukilanso. Koma pomwe pali cikhululukiro ca macimo palibenso copereka ca kwa ucimo.” Ndikukhulupilira mu Mauwa ndi mtima wanga onse, kuti Ambuye anatipulumutsadi ife ku machimo athu onse kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi Wake pamtanda.Chipulumutso Ndi Kusinthidwa Mwa Madzi Ndi Mzimu Chalembedwa Mu Mitima Yathu Ndi M’maganizo Mwathu


Okodedwa okhulupilira anzanga, kodi mukukhulupilira kuti Yesu Kristu anatipulumutsa ife motere mwakubatizidwa ndi kukhetsa mwazi Wake pamtanda? Kodi mukudzipereka nokha ku Mauwa a Mulungu mwachikhulupiliro? Ndife obadwanso mwatsopano ngati tadzipereka tokha ku Mauwa. Talandira chikhululukiro cha machio mwakukhulupilira kuti Yesu Kristu anafufuta machimo athu onse ndi Uthenga Wabwino wa chitetezero. Sikuti ndikukhala mosamara tsiku ndi tsiku komwe kwatipangitsa kulandira chikhululukiro cha machimo, koma ndikukhulupilira mu zomwe Mulungu watichitira ife kuti tilandire chikhululukiro cha machimo. Tinachotseredwa ku machimo athu onse ndikukhala anthu olungama pongokhulupilira kuti Yesu Kristu anachotsa machimo onse mu mtsinje wa Yordano pobatizidwa, ndipo kuti Iye anasenza chilango chonse pamtanda chomwe inu ndi ine tinayenera kusenza. Kodi mukukhulupilira zimenezi?

Ubatizo wa Yesu, imfa Yake pamtanda, ndi kuka Kwake kwapanga ntchito ya chipulumutso kuthekera kuti ali yense alandire chikhululukiro cha machimo ake kwa Mulungu, ndipo ndi Lamulo la chipulumutso komanso chikondi chake. Ngakhale Mulungu amatikonda ife, Iye sakonda ife ndikugwirizana nafe ngati tatsalira mu uchimo. Koma, chifukwa choti Mulungu ndi wachilungamo, Iye anapanga ife olungama kudzera mu nsembe ya Mwana Wake, mwakupanga Iye kulandira ubatizo pofuna kufufuta machimo athu onse. Pofuna kupanga ife opanda uchimo, Mulungu anatuma Mwana Wake wobadwa yekha Yesu Kristu pa dziko lino; mwakulandira ubatizo kwa Yohane Mbatizi, Atate anapereka machimo athu onse kwa Mwana Wake; ndipo mwakuweruza Mwana Wake Yesu Kristu m’malo mwathu, Atate anachotsa chiweruzo chathu. Kuti Mulungu wapanga ife kukhala opanda tchimo komanso olungama, ndi kubvomera ife monga ana ake, ndi chipulumutso chomwe Mulungu Mwini wake anabweretsa kwa ife mwa madzi ndi mwazi, ndipo ndi chikondi Chake chopanda malire.

Mulungu ananena mu Ahebri 10:16 “Ndidzapereka malamulo anga akhale pamtima pao; ndipo pa nzeru zao ndidzawalemba.” Nanga kodi ndife ochimwa mu mitima yathu ndi mnzeru zathu, kapena ndife anthu olungama? Ife tonse talemekeza Mau a Mulungu ndife anthu olungama. Yesu Kristu anachotsa machimo athu onse ndi kuweruzidwa chifukwa cha machimowo. Iye ndi Mpulumutsi. Ena a ife tingaganizebe kuti, “kodi tinganene bwanji kuti ndife anthu olungama pamene timachimwa tsiku ndi tsiku? Kodi tonse sindife ochimwa tsopano?” komabe, ngati tadzipereka tokha ku Mau a Mulungu monga Yesu Kristu anadzipereka yekha ku Mau a Mulungu, ndiye kuti tonse tizakhala olungama.

Tisanakhulupilire mu Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu, mitima yathu inali yochimwa. Komabe, pamene talandira Uthenga Wabwino wa Yesu Kristu, wa chitetezero cha machimo, tapulumutsidwa ku machimo athu onse. Pamene sitinkadziwa Uthenga Wabwinowu wa chitetezero cha machimo, tinali ochimwa. Koma tsopano takhala anthu olungama mwa kukhulupilira kuti Mulungu wapulumutsa ife kudzera mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, ndiponso mwa kudzikhuthula tokha mu chipulumutsochi. Ichi ndi chikhulupiliro chomwe mtumwi Paulo ankalankhula, chomwe munthu amakhala olungama mwa chikhulupiliro, ndipo chikhulupiliro chimenechi ndi chomwe chatipanga ife kukhala olungama mwa kukhulupilira mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo.

Mtumwi Paulo analembanso kuti Abrahamu sanakhale munthu olungama ndi tate wa chikhulupiliro mwa zochita zake, koma mwakukhulupilira Mau olankhulidwa ndi Mulungu komanso kudzipereka yekha ku Mauwa a chisomo. Monga Ahebri 10:18 akunena kuti, “Koma pomwe pali cikhululukiro ca macimo palibenso copereka ca kwa ucimo” mulungu indedi anakwaniritsa chipulumutso chathu kotheratu, kuti ife tisakhale mwa ukapolo wa uchimo. 

Pena pake mu Afilipi 2 Baibulo likunena kuti: “Mukhale nao mtima m’kati mwanu umene unalinso mwa Kristu Yesu, ameneyo, pokhala nao maonekedwe a Mulungu, sanaciyesa colanda kukhala wofana ndi Mulungu, koma anadzikhuthula yekha koma natenga maonekedwe a kapolo, nakhala m’mafanizidwe a anthu; ndipo popezedwa m’maonekedwe ngati munthu, anadzichepetsa yekha, nakhala omvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda. Mwa icinso Mulungu anamkwezetsa Iye, nampatsa dzina limene liposa maina onse, kuti mudzina la Yesu bondo liri lonse lipinde, la za m’mwamba ndi za padziko, ndi za pansi padziko, ndi malilime onse abvomere kuti Yesu Kristu ali Ambuye, kucitira umboni Mulungu Atate.” 

Podzikhutula yekha, Yesu Kristu anatenga maonekedwe a kapolo nakhala m’mafanizidwe a munthu, Iye anadzichepetsa yekha ndi kulemekeza chifuniro cha Atate nakhala omvera kufikira imfa, pofuna kupulumutsa ife tonse. N’chifukwa chake ife tikuyamika Yesu Kristu monga Mulungu wathu, Mpulumutsi wathu ndi Mfumu yathu. Tikulemekeza Mulungu Atate ndi kutamanda Yesu Kristu pa nthawi imodzi chifukwa Yesu Kristu analemekeza chifuniro cha Atate. Kukanakhala kuti Yesu Kristu sanalemekeze chifuniro cha Atate, Mwana wa Mulungu sakanalandira ulemelero. Komabe posatengera kuti ndi Mwana wa Mulungu, Yesu anadalirabe ndi kulemekeza chifuniro cha Mulungu Atate mpaka kufa. Ichi ndi chifukwa chake Iye analandira ndipo adzalandira kwamuyaya ulemelero kwa zolengedwa zonse komanso kwa anthu onse.

Baibulo linalemba kuti Yesu anakahala Mwanawankhosa wa Mulungu amene anachotsa machimo onse a dziko, pakuti Iye anasenza machimo anu onse ndi anga kudzera mu ubatizo Wake. Choncho tsopano, pafupi fupi dzaka 2000 zapita pamene Yesu anasenza machimo a dziko, ndipo inu ndi ine tinabadwa m’kati kati patatha zimenezi ndipo tsopano tikukhala m’nyengo ino. Koma ngakhale machimo amene tikuchita nthawi ino onse ali m’kati kati mwa machimo a dziko, pakuti dziko silinathe.

Popanda kusiyanitsa machimo a masiku onse ndi tchimo la chibadwidwe, kodi ife tonse sitinachimwe machimo ku umwana wathu? Ngakhale pamene tinali ana ang’ono, tinali ndi kuthekera kochita tchimo. Koma Yesu anachotsa machimo onsewa, ndipo ndi chifukwa chake Iye tikumucha Mpulumutsi wathu. Nanga kodi tinali achinyamata? Kodi sitinachitenso tchimo mu unyamata wathu? Kumene tinachita! Koma machimo onsewa anaperekedwa pa Yesu dzaka pafupi fupi 2000 zapitazo. Podziwa bwino kuti tidzachimwa kuchokera ku ubwana wathu mpaka kufa, Yesu anachotseratu machimo onse a dziko ndi kuperekeratu mphotho yake pamtanda. Tsopano, tiyeni tiganizire za moyo wa pafupi fupi dzaka 70, kodi ndi machimo angati amene tidzachimwe mu dzaka 50 dzotsatirazo? Kukanakhala kowalonga mu galimoto, tikanafunika magalimoto okwana 100 kuti adzadze bwino onse. Koma ngakhale machimo amenewa anachotsedwa kale ndi Yesu Kristu kamodzi kokha kudzera mu ubatizo Wake, ndipo Iye ananyamula machimowo kupita nawo pamtanda kubweretsa chikhululukiro cha machimo onse kwa munthu ali yense. 

Kukanakhala Yesu anachotsa tchimo lokha la chibadwa koma osati machimo a masiku onse, ndiye kuti tonse tikanakumana ndi imfa. Ngati mukuganiza kuti Yesu analephera kuchotsa machimo anu, ichi ndi chithunzi chabe cha maganizo anu. Ngakhale mukuganiza ndi kuzimva mwa inu nokha kuti Yesu sanachotse machimo onse a dziko, izo sizingasinthe zoona zakuti Yesu indedi anasenza machimo onse a dziko lapansi ndi ubatizo Wake.

Kodi ndi machimo angati amene timachimwa mu moyo wathu? Ganizirani munthu mu dzaka zake za makumi asanu. Kodi ndi mchimo angati amene iye angachimwe? Iye wachita machimo ambiri kuchokera pa nthawi imene iye anabadwa moti nzosatheka kuwerenga machimo onse. Kodi munthu ameneyu sangachite tchimo kuchokera pa nthawi imeneyo kupita kutsogolo? Ai, iye adzapitiridza ku chimwa mpaka nthawi ya kufa kwake. Machimo onsewa amachitidwa pamene tikukhala mu dziko lino posawerengera kuti anachitidwa liti, ndipo Yesu anasenza machimo onse. Ndi chifukwa chake Yesu analamula Yohane Mbatizi kuti ambatize Iye, kuti atenge tchimo lili lonse la dziko lapansi. Ambuye Mwini Wake ali ndi udindo wochitira umboni pa Iye yekha, kunena kuti, “ndachotsa machimo anu onse,” koma Ambuye sanangonena zimenezi koma anachita ntchito imeneyi. Iye anatuma kapolo wake monga oimilira wa anthu onse, ndipo kudzera mwa munthu ameneyu, Yesu anawerama mutu Wake kwa Yohane Mbatizi ndipo Iye anabatizidwa ndi iye, Ambuye anapanga chitetezero cha machimo onse a anthu, machimo onse a dziko, komanso machimo athu onse. Iye anapanga chitetezero cha tchimo lili lonse lomwe tachita komanso lomwe tidzachite mu moyo wathu onse, komanso machimo onse amene mbumba yathu idzachite. Amene anachotsa machimo onse a mtundu onse wa anthu ndi ubatizo Wake ndi Yesu Mpulumutsi wathu.

Nanga ndindani amene anganene kuti kudakali machimo mu dziko lino? Ambuye anachotsa machimo onse mu njira imeneyi, ndipo ngati ife takhulupilira mu zomwe zinakwaniritsidwa ndi Yohane Mbatizi komanso Yesu kuchokera pansi pa mitima yathu ndi chitsimikizo, ndiye kuti tonse ife tidzaomboledwa ndi kupulumutsidwa ku machimo athu onse.

Nthawi zina ndimakamba pa zomwe ndakumana nazo kwambiri, ngati kuti ndine ndekha amene ndadutsa moyo obvuta, koma ndikudziwa kuti pali anthu ambiri amene adutsa moyo obvuta kwambiri, ndipo kutinso ambiri a inu mwabvutika kwambiri mu moyo wanu. Kodi ndi chifukwa chakuti moyo ndi wautali kuti timakumana ndi zokhoma zambiri? Ai. Mulungu akunena kuti masiku athu anadutsa mkwiyo Wake ndipo timamaliza dzaka dzathu monga mpheya (Masalmo 90:9). Ndipo Mulungu akupitiliza kunena kuti myoyo yathu ndi yopanda ntchito, ponena kuti, “Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi awiri, kapena tikakhala nayo mphamvudi zaka makumi yasanu ndi atatu; koma teronso kukula kwao kumati cibvuto ndi copanda pace; pakuti kumapitako msanga ndipo tithawe ife tomwe” (Masalmo 90:10). 

Lolani ndigwiritse ntchito ntchentche kuti ndiunikire nfundo yanga. Theka la moyo wa ntchentche ndi maora khumi ndi awiri. Ntchentche zimakhala tsiku limodzi ndichifukwa chake zimatchedwa kuti youluka tsiku limodzi. Choncho tsopano, ganizani kuti mulu wa ntchentche wabwera pamodzi masana utatha kukhala maora khumi ndi awiri ndi kuyamba kukabitsana okha okha za ulendo wao komanso zomwe apitamo pa nthawi ya maora khumi ndi awiri. Pakuri ntchentche, kukhala maora khumi ndi awiri zikutanthauza kuti zakhala theka la moyo wao. Polowa dzuwa, ndiye kuti zakhala 2/3 (magawo awiri mwa atatu) a moyo wao, ndipo zingakambe za m’mene zakalambira kufikira kumapeto awo. Zambiri za izo zingayambe kuonongeka mdima ukangoyamba, ndipo ngakhale ntchentche ya moyo wautali ingafe pakati pausiku. Kukanakhala komvetsera zokamba zao ndikumva izo zikukamba pakati pao za zomwe akumana nazo maora makumi awiri ndi anayi, tikanaseka pa izo popeza moyo wathu ndi okhala pakati pa zaka makumi asanu ndi awiri kufikira makumi asanu ndi atatu. Monga m’mene ntchentchezi ziri zoseketsa kwa ife, choncho ndi m’mene Mulungu amationera ife. 

Popeza Mulungu anaganiza chiyambi ndi mathero a dziko, Iye ndi wakukhala kwamuyaya, Iye akukhala mu nthawi yosatha Mulungu amatiyang’ana ife mopanda nthawi. Kalekalo, Mulungu yekha anadza padziko lino, ndi kupanga chitetezero cha machimo a mtundu onse wa anthu mu dziko lino, Iye anasenza machimowo kudzera mu ubatizo Wake ndi kufa pamtanda, kunena kuti, “kwatha!” Iye kenako anauka kwa akufa m’masiku atatu ndi kukwera kumwamba. Mulungu tsopano akukhala m’maora opanda nthawi. Ndipo Iye akutiyang’anira ife kuchokera ku nthawi Yake yosatha. Ndiloleni kuti ndifanizire ndi chitsanzo china.

Tiyeni tiganizire kuti wina wake akuganiza kwa iye yekha, “ndiri ndi dzaka makumi atatu zakubadwa, koma ndachita kale machimo ambiri. Ndikuchita mantha kuti ndidzachita ngakhale machimo ambiri zaka zikubwerazo. Nanga kodi ndingakhululukidwe bwanji?” Ambuye wathu, amene akukhala mu nyengo yosatha, adzanena kwa munthuyu, “kodi ukundichepetsa Ine? Nzopanda nzeru! Kodi ukuganiza kuti ndinachotsa machimo amene wangochita pamenepa? Kodi ukuganiniza kuti ndiye machimo okhawo amene ndinachotsa? Ndinachotsa machimo onse a dziko! Ndinalandira machimo onse a munthu ali yense pa thupi Langa, kuchokera kwa Adamu munthu oyamba kufikira kwa munthu omaliza kuimilira kutha kwa dziko, kuphatikiza machimo onse a mbumba yako!” pokhala m’maora Ake opanda nthawi, Ambuye anati Iye anasenza machimo onse a mtundu wa anthu kuti apereke chikhululukiro cha machimo athu onse.Ambuye Wakwaniritsa Chipulumutso cha Ochimwa Aliyense Kotheratu


Tiyeni tione pa Yohane 19:17-20 apa: “Ndipo anasenza mtanda yekha, naturuka kunka ku malo ochedwa Malo a-bade, amene achedwa m’Cihebri, Golgota: kumene anampacika Iye; ndipo pamodzi ndi Iye awiri ena, cakuno ndi cauko, koma Yesu pakati. Koma Pilato analemba limbo, naliika pamtanda. Koma panalembedwa, YESU MNAZARETI, MFUMU YA AYUDA. Ndipo limbo ilo analiwerenga ambiri a Yuda; cifukwa malo amene Yesu anapacikidwapo anali pafupi pa mudziwo; ndipo linalembedwa m’Cihebri, ndi m’Ciroma, ndi m’Cihelene”

Atasenza machimo onse a dziko, Yesu Kristu analamulidwa kukaphedwa pa bwalo la Pilato ndi kupachikidwa. Tiyeni tiyang’ane pazimenezi pang’ono apa. Kwalembedwa mu Yohane 19:28-30: “Citapita ici Yesu, podziwa kuti zonse zidatha pomwepo kuti limbo likwaniridwe,” Yesu anachotsa machimo athu onse kuti lemba likwaniridwe. “Ananena, Ndimva ludzu. Kunaikidwako cotengera codzala ndi vinyo wosasa; cifukwa cace anazenenga cinkhupule codzadza ndi vinyo wosasayo pa phesi lahisope, nacifikitsa kukamwa kwace. Pamene Yesu tsono adalandira vinyo wosasayo anati, Kwatha; ndipo anawerama mutu, napereka mzimu.”

Yesu Kristu anasenza tchimo lililonse malingana ndi malembo. Atalandira vinyo osasa, Yesu Kristu anati, “kwatha!” ndipo anawerama mutu Wake, kenako anafa, koma Iye anauka kwa akufa mu masiku atatu ndi kukwera kumwamba. Ubatizo omwe Yesu analandira kwa Yohane Mbatizi komanso imfa yomwe Iye anazunzika pa mtanda zinali zofunika ndi zogwirizana pamodzi ku chikwaniritso cha uthenga wabwino wa chitetezero cha machimo. Ndikuthokoza kwa Ambuye populumutsa ife motere kudzera mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo.

Komabe, thupi la aliyense limatsatirabe zomwe thupi likufuna. Choncho, muthupi ali yense ndi ochimwa poti amaphwanya malamulo a Mulungu ndi kuchimwira Iye moyo wake onse, ndipo tonse tili ndi thupi lofanana. Koma kwa anthu ngati ife, Ambuye wathu anabweretsa chipulumutso cha ubatizo ndi mwazi wa Yesu, omwe Iye anachotsa machimo athu onse. Mulungu anatipulumutsa motere. Pobadwira mu Betelehemu, Yesu anasenza machimo onse adziko mu mtsinje wa Yordano kudzera mu ubatizo wake, ndipo Iye tsopano wapanga kuthekera kwa onse amene alandiradi chitetezero cha machimo kulowa Ufumu Wakumwamba mwa chikhulupiliro mthawi ili yonse, poti anthu amenewa akhulupilira mu Uthenga Wabwino wa madzi, mwazi, ndi kuuka kwa Ambuye. Ndikupereka kulemekeza konse kwa Ambuye, matamando ndi chiyamiko.Yesu Anabwezeretsa Chikhulupiliro cha Petro


Pamene tabvundukula pa chapta chomaliza mu Uthenga Wabwino wa Yohan, tikuona kuti Yesu anapita ku Galileya pamene Iye anauka. Iye anapita kukayang’ana Petro, ndipo pamene anampeza Iye Iye anamfusa iye, “Simoni, mwana wa Yona, kodi undikonda Ine koposa awa?” Petro kenako anamuyankha Iye nati, “Inde, Ambuye; mukudziwa kuti ndikukondani Inu,”ndipo anayankha mombwezera, “Dyetsa ana a nkhosa anga.”

Chikhulupiliro cha Petro pomaliza pake chinakwanira pa nthawiyo, ndi mtima wake anazindikira Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo opangidwa ndi ubatizo komanso mwazi wa Yesu. Chikhulupiliro chake mwa Ambuye chinalimba koposa, Petro tsopano anazindikira chifukwa chimene Ambuye anatsukira mapazi ake, kumvetsetsa Uthenga Wabwino wa madzi ndi mwazi, ndi kukhulupilira mu Uthenga Wabwinowu wa chitetezero cha machimo.

Tiyeni tibvundukule pa Yohane 21:15-16 apa ndi kuona zomwe Yesu ananena kwa Petro pamene Iye anaonekera kwa ophunzira pamene Iye anauka: “Ndipo pamene atafisula Yesu ananena kwa Simoni Petro, ‘Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine koposa awa? Ananena ndi Iye, Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Dyetsa ana a nkhosa anga.’”Ndimeyi ikutiza ife kuti Ambuye angadalire tsopano petro kugwira ntchito kwa anthu Ake, pakuti Petro ndi ophunzira amene wapulumutsidwa kotheratu komanso wakhala mtumiki olungama wa Mulungu wangwiro.

Kukanakhala kuti Petro anatembenuka kukhala ochimwa kachiwiri chifukwa chakuti iye anachita tchimo mu thupi lake, ndiye kuti Ambuye sakanadalira Uthenga Wabwino wa Madzi ndi Mzimu, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo onse, kwa Petro kapena kwa ophunzira ena omangidwa ndi machimo awo amasiku onse a kuthupi. Koma Ambuye anadalira Petro komanso ophunzira ena ku ntchito ya Uthenga Wabwino wopanga chitetezero cha machimo onse, chifukwa iwo onse anakhulupilira mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo operekedwa ndi Mulungu, mu ubatizo wa Yesu komanso mwazi wake pamtanda.“Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu” 


Tiyeni tiwerenge kachiwiri zomwe Ambuye akunena kwa Petro: “Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine koposa awa?” Petro kenako anamuyankha Iye nati, “Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu.” Kuulula kwa chikhulupilirochi kunapangidwa ndi Petro chifukwa iye akhulupilira mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo omwe Ambuye anampatsa iye.

Kukanakhala kuti Ambuye sanamuuze Petro komanso ophunzira ena za Uthenga Wabwinowu wa chitetezero cha machimo mu Yohane 13 pamene Iye ankatsuka mapazi ao, ndi kuonekera kwa Petro pamene Iye anauka ndi kumfunsa iye, “kodi undikonda Ine koposa awa?” kodi Petro akanayankha bwanji? Iye akananena kuti, “ndili ndi zolakwa zambiri. Ndine ochimwa, sindingakwanitse kukukondani kuposa anthu onsewa. Chonde, ndisiyeni ndekha.” Petro kenako anathawa ndi kumusiya Yesu.

Petro, komabe, yankho losemphana kotheratu, poti iye anabvala chisomo cha Ambuye cha Uthenga Wabwino wa chipulumutso, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo omwe unakwaniritsidwa ndi ubatizo komanso mwazi wa Yesu. Tiyeni timbvetsere mwatcheru komaliza pa zomwe Petro ananena mu yankho lake: “Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu.” Kuulula kwa chikhulupilirochi kunapangidwa chifukwa Petro anakhulupilira mua Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimochomwe Ambuye anampatsa iye. Pokhulupilira mwa Yesu Kristu monga Ambuye wake, Petro tsopano anakhulupilira kuti Ambuye anafufuta machimo onse omwe iye anachimwa ndi manja komanso mapazi kamba ka kufooka kwake- ndiye kunena kuti, iye anakhulupilira mu Uthenga Wabwino wa Mulungu wa chikhululukiro cha machimo kwa muyaya. Chifukwa Petro anakhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Mwanawankhosa wa Mulungu, iye anali ndi kuthekera kokhulupilira mu chipulumutso cha Ambuye komanso chikondi chake, ndipo kachiwiri kuulula chikhulupiliro chake. Chipulumutso cha Petro ku machimo ake chinachokera ku Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo opangidwa ndi ubatizo ndi mwazi wa Yesu, ndipo choncho iye akanapulumutsidwa ku kotheratu ku machimo ake amasiku onsenso. Chikhulupiliro chake chinaikidwa mu chipulumutso chomwe chinabwera ndi Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, chomwe chinakwaniritsidwa kudzera mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu Kristu.

Nanga inu bwanji? Kodi mukukhulupiliranso ngati m’mene Petro ankakhulupilira? Popatsidwa choona choti Ambuye anafufuta machimo onse a dziko ndi Uthenga Wabwino wa chikhululukiri cha machimo athu, mwa kubatizidwa ndi kukhetsa mwazi wake, kodi ife tonse sitikanakhulupilira Ambuye ndi kusamukonda Iye? Kodi sitikanakhulupilira bwanji mu ubatizo wa Ambuye ndi mwazi omwewapanga chitetezero cha machimo athu onse, nanga tikanakhala bwanji osamukonda Iye? N’zosatheka kusamukonda Iye! Kukanakhala kuti Ambuye sanapange chitetezero cha machimo athu onse, ndipo m’malo mwake kuchotsa machimo akale okha kapena atsopano koma osati machimo athu amtsogolo, ndiye kuti sitikanatamanda Ambuye pa chipulumutso chake. Ndipo aliyense akanaweruzidwa kukhala ku gahena mudziko lino komanso dziko liri nkudza. Choncho tsopano, onse a ife tiyenera kubvomereza kuti tapulumutsidwa mwa kukhulupilira mu Uthenga Wabwino omwe wabweretsa chikhululukiro cha machimo athu onse amasiku onse. Tiyenera kubvomereza kuti thupi lathu mthawi zonse limatsata uchimo, omwe timachita mopitilira mu thupi lathu pa chifukwa ichi, ndipo kuti motero tapulumutsidwa ku machimo onse mwa kukhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo omwe Yesu anatipatsa ife.

Tikanakhala kuti sitinakhulupilire mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake, Uthenga Wabwino wa chikhululukiro cha machimo onse, ndiye kuti palibe m’modzi wa ife amene akanapulumutsidwa ku machimo amasiku onse. Ndipo tikanakhulupilira mu mwazi okha wa Yesu wa pamtanda ndi kulandira chikhululukiro cha machimo mwa kupemphera mapemphero a kulapa nthawi zonse pamene tachimwa, ndiye kuti zikanatipanga ife a ulesi kukwaniritsa izi, komanso zikanatheka kwa ife kukhala ndi uchimo mu mtima mwathu nthwawi zonse. Zikanati izi zachitika, ndiye kuti tikanakhalanso ochimwa kachiwiri; zikanakhala zosatheka kwa ife kumkonda Ambuye komanso zikanakhala zotibvuta ife kumuyandikira Iye; komanso; mwachidziwikire, sitikanakhulupilira mu chipulumutso cha ndi Ambuye kulephera kutsatira Iye mpaka kumapeto.

Komabe, Ambuye wathu watipatsa Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo onse a mtundu onse wa anthu ndi kupulumutsa ali yense amene wakhulupilira mu Uthenga Wabwinowu. Pokhala Mpulumutsi wangwiro, Iye wachotsa machimo onse a masiku onse omwe ife timachita mu thupi lathu tsiku lili lonse, ndipo pamene Iye watipats ife Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, watipanga ife kuti timkonde Iye. Tsopano sitingadzithandize koma kukonda Uthenga Wabwino wa ubatizo ndi mwazi wa Yesu omwe wabweretsa chitetezero cha machimo. Ali yense amene wakhulupilira mu Uthenga Wabwinowu anapangidwa kukonda Ambuye kwamuyaya monga mkaidi wa chikondi cha Ambuye omangidwa ku Uthenga Wabwino, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo onse.

Kukanakhala kuti Ambuye anasiya kachidutswa ngakhale kakang’ono, ndiye kuti simunakakhulupilira mwa Ambuye kapena kukhala mboni ya Uthenga Wabwino wa Ambuye wa chitetezero cha machimo kugwira ntchito ngati mtumiki wa Ambuye.koma ngati mwakhulupilira mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo chomwe Ambuye anakwaniritsa, mudzapulumutsidwa ku machimo onse. Ambuye wapanga kuthekera kwa inu kuti mupulumutsidwe ku machimo onse. Ngati mwazindikira Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo olembedwa m’Mau a Yesu monga chipulumutso chake changwiro, mudzapulumutsidwa ku machimo onse a dziko.“Kodi Undikonda Ine Koposa Awa?” 


 Mulungu wadalira anaankhosa Ake kwa anthu Ake komanso akapolo ameneme akhulupilira mu Uthenga Wake Wabwino wachitetezeroo cha machimo. Ambuye anafunsa Petro kosachepera katatu, “Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine?” ndipo Petro anamuyankha Iye, “Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu.” Tiyenera kumvetsera kuyankholi mwatcheru. Yankholi silinachokere kuchifuniro cha Petro, koma lizikika kuchokera ku chikhululukiro cha Petro mu Mau a Uthenga Wabwino wachitetezero cha machimo onse omwe Ambuye anampatsa iye. Pamene takonda Anbuye, ngati chikondichi chagona pa zifuniro za zikhulupiliro zathu, chidzasowa pamene tapunthwa kamba ka kufooka kwathu, koma ngati chikondi chathu pa Ambuye chidalira chikondi Chake pa ife, ndiye kuti chikondi chathuchi chidzakhalanso kwamuyaya. Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu ndi chitetezero cha machimo, ndipo ndi Uthenga Wabwino wa ngwiro omwe wapulumutsa ife.

Kuti ife titumikire Mulungu monga atumiki Ake ndi kumukonda Iye, kudzikhuthula kwathu kuyeneranso kugona pa chikhulupiliro chathu mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo. Kukanakhala kokhulupilira mwa Mulungu pogona mu chikhulupiliro cha zofuna zathu, ndiye kuti pambuyo pake tikanapunthwa ndipo zotsatira zake tikanada chikhulupiliro chathu ndi kuchisiya, koma Ambuye anachotsa machimo athu obadwa nawo, amasiku onse, amtsogolo, komanso machimo a kuthupi ndipo chipulumutso Chake chafufuta machimo onse a ali yense pa dziko lino popanda kuchotsera, kuphatikizanso Petro.

Indedi, kukanakhala kodalira pa chifuniro chathu, chikondi chathu, komanso zikhulupiliro zathu, kukanakhala kosabvuta kwa ife kulephera mu myoyo yathu yachikhulupiliro, koma ngati tidalira pa Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo omwe Ambuye anatipatsa ife, tizakhala moyo wapamwamba wachikhulupiliro monga iwo amene apulumutsidwa pongokhulupilira mwa Ambuye ndi mitima yathu. Takhala tsopano ana a Mulungu komanso anthu olungama. Chifukwa takhulupilira mu chipulumutso cha madzi ndi Mzimu, ndife anthu osachimwa, ndipo chifukwa chipulumutso chathu sichinapezeke pokhulupilira mwa ife tokha koma pokhulupilira mu chikondi cha Ambuye komanso Lamulo Lake loona la chipulumutso ndi chitetezero cha machimo, ndife okhulupilira olungama ndipo tidzakhala choncho kwamuyaya posatengera zolakwa zathu; tidzakhala moyo wathu wachikhulupiliro monga iwo okonzedwera kumwamba; kutamanda Mulungu kwamuyaya; ndi kulowa Ufumu wa kumwamba kuyamika Mulungu. Kodi nonse mukukhulupilira mu zimenezi?

Yesu anati “Si inu amene mwakonda Ine koma ndi Ine amene ndakonda inu,” pakuti Baibulo likunena kuti, “Umo muli cikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti Iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana Wace akhale ciombolo cifukwa ca macimo athu” (1 Yohane 4:10). Tsopano, ngati Yesu wapulumutsa ife kudzera mwa madzi ndi Mzimu, ndiye kuti ife tiyenera kukhala ndi chikhulupiliro mu ubatizo Wake ndi mwazi, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo. Kukanakhala kuti Mulungu sanapulumutse ife kudzera mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, zitikanapeza chipulumutso ngakhale tikanakhulupilira bwanji mwa Mulungu. Koma kudzera mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, Ambuye wapulumutsa ife kumachimo onse a ku thupi.

Kuti takhulupilira mwa Mulungu, kuti takhala anthu olungama, ndipo kuti tapulumutsidwa-zonse izi ziyenera kutsimikizidwa ndi kukhulupira mu Mau a Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu, Uthenga Wabwino omwe wabweretsa chikhululukiro cha machimo athu. Chikhulupiliro chomwe chimabweretsa chikhululukiro cha machimo athu ndi chikhulupiliro chozikika mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Uthenga Wabwinowu wa chitetezero cha machimo ndi Uthenga Wabwino wa choonadi, chinthu cheni cheni cha chipulumutso, komanso nkhani yeni yeni ya malembo.Muyenera Kuika Pambali Chikhulupiliro Cha Chifuniro Chanu


Chikhulupiliro chanu cha chifuniro chanu sichikhulupiliro cheni cheni, kapena chikondi cha chifunirochanu sichikondi cheni cheni. Zilibe ntchito poti ndi chifuniro chanu komanso kutengeka kwanu. Komabe pali anthu ambiri mu dziko lino amene akukhulupilira mwa Yesu poyamba pogonera pa kumva bwino kwao, pongomangidwa ndi uchimo komanso pamapeto pake kuleka chikhulupiliro chao. Komabe, Ambuye wathu anatipulumutsa ife ku machimo onse a masiku onse, akulu ndi ang’ono pamodzi, kaya ochitidwa modziwa kapena mosadziwa. Choncho, pofuna kuphuzitsa ophunzira za m’mene Iye wafufutira machimo ao onse kotheratu, Yesu anawasonkhanitsa pamodzi Iye asanafe, ndipo pamene anadya mgonero ndi iwo, Iye anathira madzi mbeseni ndi kutsuka mapazi a ophunzira, monga ationetsa mu Yohane 13. Tonse a ife tiyenera kudziwa Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo obvumbulutsidwa m’malemba a ndimeyi ndikukhulupilira mwa iwo.

Poyamba, Petro anakana Yesu mosabweza maganizo ake ndi kunyala nyaza kuti mapazi ake atsukidwe ndi Ambuye, konena kuti, “simudzasambitsa mapazi anga ku nthawi yonse!” Izi zikuonetsa za m’mene chifuniro cha chikhulupiliro cha Petro chinalili. Koma Yesu ananena ndi iye, “Cimene ndicita Ine, sucidziwa tsopano; koma udzadziwa m’tsogolo mwace.” Kudzera mu Uthenga Wabwino wa Yesu wa madzi ndi Mzimu, tazindikira tsopano Mau omwe Ambuye analankhula kwa ophunzira. Mauwa ndi Mau a choonadi, ndipo ochimwa ali yense adzapangidwa olungama pokhulupilira mu Mau a madzi ndi Mzimu, Uthenga Wabwino wachitetezero cha machimo onse omwe Ambuye anatipatsa ife.

Tsiku lina, Ambuye atauka, Petro anali mu Nyanja ndi ophunzira ena kuwedza. Iwo anabwerera ku ntchito zao za kale, koma pamene ankawedza nsomba, Yesu anaonekera mphepete ndipo anawaitana iwo. Pa nthawiyo Yesu anali atakonzekera kadzusa wa ophunzirawo, ndipo pamene ankadyera pamodzi, Petro pomaliza anamvetsetsa zomwe Yesu ankatanthauza pamene Iye ananena kwa iye pamene ankatsuka mapazi ake pa tsiku la Paskha, “Cimene ndicita Ine, sucidziwa tsopano; koma udzadziwa m’tsogolo mwace.” Pa mbuyo pake zinazindikirika kwa Petro, “Yesu anachotsadi machimo anga onse. Podziwa kuti ndidzachimwanso chifukwa cha kufooka kwanga, Iye anachotsa machimo anga amtsogolo.” Tsopano pamene iye analeka chifuniro chake ndi chilungamo chake, Petro tsopano anakhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu, Uthenga Wabwino wa Ambuye wa chitetezero cha machimo onse, ndi kumuyamika Iye populumutsa iye.

Atamaliza kudya kadzutsa, Yesu anafunsa Petro, “Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine?” pa nthawiyo, Petro anaimilira tsopano pa chikhulupiliro chake chosasintha mu chikondi cha Ambuye ndi kuulula, “inde, Ambuye; Inu mukudziwa kuti ine ndikukondani.” Petro anazindikira tanthauzo leni leni la zomwe Yesu ananena kwa iye pamene Iye ankatsuka mapazi ake, ndi kukhulupilira m’Mau amenewa-“ Cimene ndicita Ine, sucidziwa tsopano; koma udzadziwa m’tsogolo mwace.” Ndipo ndi chifukwa chake Iye anabvomereza chotere kuonetsa chikhulupiliro chake choonadi mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, chitetezero cha machimo. Pambuyo Pake, Petro Anakhala Mtumiki Weni Weni Wa Mulungu


Choncho kunali, patatha zimenezi, Petro ndi ophunzira onse analalikira Uthenga Wabwino kwa ochimwa mpaka imfa yao. Ngakhale mtumwi Paulo, amene anazunza ndi kupha Akristu, anachitiranso umboni za Yesu pansi pa ulamuliro wankhanza wa Aroma. Kwa ophunzira khumi ndi awiri omwe anapezeka pa m’gonero, Yudase anampereka Yesu ndi kudzimangilila yekha pamapeto pake, ndipo mtumwi Paulo anatenga malo ake m’malo mwake. Ngakhale ophunzira ankafuna kusinthanitsa Matiyasi ndi Yudase, Mulungu anasankha mtumwi Paulo, ndipo Paulo anakhala ophunzira wa Yesu ndi kulalika Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo onse pamodzi ndi atumwi ena.

Ophunzira onse a Yesu anaphedwa. Ndipo mpaka pa nthawi ya kuphedwa kwao, iwo onse analalika Uthenga Wabwino oyamba, kunena kuti, “ndi Uthenga Wbwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, chitetezero cha machimo, Yesu Kristi anafufuta machimo anu onse a thupi. Mwakubatizidwa mu mtsinje wa Yordano, Iye anasenza machimo onse a dziko pa thupi Lake, ndipo mwa kukhetsa mwazi Wake pamtanda, Iye anaweruzidwa m’malo mwanu. Khulupilirani mu Uthenga Wabwinowu wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pamtanda monga chipulumutso chanu ku machimo anu onse. Khulupilirani ndi kupulumutsidwa.” Anthu osawerengeka anamva ndi kukhulupilira mu Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu olalikidwa ndi ophunzira, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, ndipo zotsatira zake onse anapulumutsidwa. Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu, ubatizo ndi mwazi wa Yesu, unali Uthenga Wabwino omwe unali ndi mphamvu yeni yeni ya chikhulupiliro. 

Ophunzira anaperekera umboni wa Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu, kulalikira kuti, “Yesu ndi Mulungu. Iye ndi Mpulumutsi wanu.” Zikomo chifukwa cha umboni umenewu wa Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu olalikidwa ndi ophunzira, inu ndi inenso tamva Uthenga Wabwino umenewu wa chipulumutso, ndipo ife tapulumutsidwa pokhulupilira mu Uthenga Wabwino umenewu wa ubatizo ndi mwazi wa Yesu omwe wabweretsa chikhululukiro cha machimo. Ndipo pa chikondi cha Mulungu kmanso chipulumutso cha ngwiro cha Yesu Kristu, ifenso takhala ophunzira Ake.

Kodi inu mukukhulupilira mu zonsezi, okondedwa okhulpilira anzanga? Ndi chikwa chakuti Mulungu anatikonda ife motere kuti takhala anthu olungama ndi ophunzira a Yesu Kristu. Kunali kuphunzitsa Uthenga Wabwino wa choonadiwo wa chitetezero cha machimo ndi chipulumutso choonadi kuti Yesu anatsuka mapazi a Petro ndi mapazi a ophunzira ena. Iye anatsuka mapazi a ophunzira Ake pofuna kuphunzitsa ife Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, kale kalero, ndi ubatizo Wake ndi mwazi, Yesu anatsuka kale machimo onse a dziko ochitidwa mu thupi lathu moyo wathu onse. Ndi kutokoza Ambuye pa Uthenga Wake Wabwino ndi chikondi Chake. 

Kodi ndi chifukwa chiani Yesu potsuka mapazi a ophunzira Ake kukufotokozedwa muzigawo ziwiri? Choyamba, monga Ambuye wathu ananena kwa Petro pamene ankatsuka mapazi ake, “Cimene ndicita Ine, sucidziwa tsopano; koma udzadziwa m’tsogolo mwace” Iye anafuna ife kuti tidziwe kuti Iye anafufuta machimo athu onse ndi ubatizo Wake komanso mwazi, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo. Cha chiwiri, Yesu anafuna ife kuti titsate chisanzo Chake. Yesu ndi Ambuye wathu ndipo Iye wapulumutsa ife ochimwa ndi kutipanga ife olungama potumikira ife-ndipo kunena kuti, Iye anatumikira ophunzira Ake mwa kutsuka mapazi ao ndi kulalika Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo kwa iwo. Motere, monga Ambuye anapulumutsa ife, choncho oyamba pakati pa ife ayenera kutumikira otsiriza. Pali zifukwa ziwiri zomveka bwino chifukwa chimene Yesu anatsukira mapazi a ophunzira Ake pa chikondwerero cha Paskha mu Yohane 13, ndipo izi ndi zofunikirabe kwambiri ku mpingo wa Mulungu.

Yesu anati, “Pakuti wamkuru ndani, iye wakuseama pacakudya kapena wakutumikirapo? Si ndiye wakuseama pacakudya kodi? Koma Ine ndiri pakati pa inu monga ngati wotumikira” (Luka 22:27). Monga Ambuye wathu ananena apa, tikulalika Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu mu dziko lonse mwakudzipereka tokha ngati unsembe kutumukira mpingo wa Mulungu, kuti iwo amene alandira chikhululukiro cha machimo kudzera mu utumuki wathu atsate mapazi yathu. Kunali kuphunzitsa ife pamene Ambuye wathu anatsuka mapazi a ophunzira. Ndipo pophunzitsa ife Uthenga Wabwino wakale momveka bwino ndi kupanga chitsimikizo kuti ife tisanyengedwe ndi satana, Ambuye anaonetsa kwa ife kudzera mukutsambitsa mapazi a Petro pachikondwerero cha Paskha, kuti Iye anakhala Mpulumutsi wathu wa ngwiro. Okhawo a inu amene mwakhulupilira kuti Yesu anatsuka machimo anu onse kudzera mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, ndi kukhulupilira mu Uthenga Wabwinowu wa ubatizo ndi mwazi wa Yesu, imfa Yake, ndi kuuka Kwake, angapulumutsidwe ku machimo onse a dziko mwa chikhulupiliro. Mwapulumutsidwa Pokhulupilira Mu Uthenga Wabwino Omwe Watsuka Machimo Anu Onse Amasiku Onse


Pongokhulupilira mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, Mau a madzi ndi Mzimu, tingapewe tokha ku chinyengo cha satana. Ndi zosabvuta kwa ife kunyengedwa ndi mdierekezi pamene iye akunena kuti, “umachita tchimo mu thupi lako nthawi zonse, ndipo tsopano ungakhale bwanji opanda tchimo? Kodi sindiwe ochimwa?” koma ife tingaime molimbana ndi mdierekezi ndi kunena kwa iye, “kudzera mu ubatizo Wake, Yesu anachotsa machimo onse omwe ndi machita mu thupi langa. Nanga kodi ine, amene ndi makhulupilira mu zimenezi, ndingakhale bwanji ochimwa? Ambuye anapereka kale mphotho yonse ya machimo anga, nanga tsopano ndingakhale bwanji ndi ngongole ili yonse yotsala?” ngati mungaone mau a mdierekezi popanda kukhulupilira mu Uthenga Wabwino wa madzi ndi mwazi wa Yesu Kristu, ndiye kuti angaoneke monga iye akunena zoona, koma ngati mwakhulupilira mu Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu, ndiye kuti Mau a choonadi a Mulungu ndi olondora. Ndichifukwa chake muyenera kukhulupilira mu Uthenga Wabwino omwe ukulola inu kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Chikhulupiliro ndicho kukhulupilira mu Uthenga Wabwino olembedwa wa ubatizo wa Yesu, mwazi Wake pamtanda, imafa Yake ndi kuuka Kwake.

Kodi munaonapo chithunzi cha pachihema? Bwalo la chihema linazunguliridwa ndi makoma a zithunzi oikidwa pa zipilala. Ndipo mkati la bwalo, munali nyumba ya golide. Nyumbayi inagawidwa magawo awiri. Inagawidwa m’malo oyera kunja otchedwa malo opatulika komanso malo oyera mkati otchedwa malo opatulikitsitsa, momwe munali mpando wa Chifundo wa Mulungu. Bwalo la kachisi lomwe Mulungu ankakhala linazunguliridwa zipilala 60. Ndipo malo opatulika inali nyumba yomangidwa ndi matabwa a golide 48. Ndikofunika kwa ife kuti tikhale ndi kumvetsetsa za m’mene chihema chinkaonekera, pakuti zizatithandiza ife kumvetsetsa zomwe Mulungu akunena kwa ife kupitira mu chihema.Kodi Zipangizo za Chipata Cha Bwalo la Chihema Zinali Zotani?


Za chitseko la bwalo la kachisi, kunalembedwa mu Eksodo 27:16, “Ndipo pa cipata ca bwalolo pakhale nsaru yotsekera ya mikono makumi awiri, ya lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, nchito ya wopikula; nsici zake zikhale zinai, ndi makamwa ao anai.” Zipangizo zomwe zinagwiritsidwa ntchito kupanga chipata cha bwalo la kachisi zinali la lamadzi, lofiirira, lofiira, komanso bafuta wa thonje losansitsa. Chipata cha bwalo, chomwe chinayezedwa mamitala 2.5 m’mwamba komanso mamitala 10 mulifupi, chinapangidwa mokongola komanso modabwitsa ndi zipangizo zinai zimenezi za lamadzi, lofiirira komanso lofiira ndi bafuta la thonje losansitsa. 

Monga chipata cha bwalo la kachisi chinali chokutidwa ndi nsaru lamadzi, lofiirira. Komanso ndi lofiira ndi bafuta wa thonje losansitsa, Mulungu anapanga chidziwitso chakuti ali yense achipeze mosabvuta ndi kulowa mkati. Khomo la kachisi linali lokutidwa ndi nsaru lamadzi, lofiirira komanso lofiira ndi bafuta wa thonje losansitsa (Eksodo 26:36). Nsaru lamadzi, lofiirira, lofiira ndi bafuta wa thonje losansitsa logwiritsidwa ntchito pachitseko cha kachisi komanso pa chipata cha bwalo lake chinali chikonzero cha Mulungu cha chipulumutso kulonjeza kuti Iye adzapulumutsa okhulupilira Ake onse kudzera mu ubatizo, mwazi ndi umulungu wa Mwana Wake Yesu Kristu. Zipilala zonse 60 zozungulira bwalo la kachisi, nsaru zonse, mitundu, komanso zipangizo zogwiritsidwa ntchito pamenepo zonse ziri ndi kufunika kwa padera, ndipo zonse zikulankhula chilungamo chakuti Mulungu Atate adzapulumutsa ife kudzera mwa Mwana Wake Yesu Kristu.

Tsopano, kodi ndi zipangizo zingati zomwe zinagwiritsidwa ntchito kumanga chipata cha bwalo la kachisi? Mitundu inai ya nsaru inagwiritsidwa ntchito-lamadzi, lofiirira, komanso lofiira ndi bafuta wa thonje losansitsa. Mitundu inai imeneyi ndi zinthu zofunika zomwe ndi zoyenereka kwa ife kukhulupilira mu Uthenga Wabwino wa kusinthidwa. Zikanakhala kuti ndi zosafunika, Baibulo silikanazilemba izo mdongosolo. Chitseko cha kachisi ndi chipata cha bwalo lake zinapangidwa ndi nsaru la lamadzi, lofiirira ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje chifukwa zikutanthauza zinthu zofunika komanso zoyenera kwa Mulungu kupulumutsa ife ku machimo a masiku onse, a chibadwidwe komanso akutsogolo. Umu ndi m’mene Mulungu anakonzera. Ndi chifukwa chake Iye anabvumbulutsa chisanzo cha kachisi kwa Mose poyamba ndi kumuuza iye kuti apange kachisiyo chimodzi modzi monga anamuonetsera iye. Kodi Nsaru Lamadzi, Lofiirira, Komanso Lofiira Zikutanthauza Chiani mu Uthenga Wabwino wa Mulungu?


Muyenera kuzindikira poyamba kuti chitsanzo cha kachisi akutanthauza chithunzi chatsatane tsatane cha Yesu Kristu: amene Iye ndi, amene watipulumutsa ife anthu olungama. Mkati mwa chihema chinsaru china chinapangidwa ndi lamadzi, lofiirira, komanso lofiira ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndipo chinsaruchi chinaikidwa pakati pa malo oyera ndi malo oyeretsetsa. Komanso mikanjo ya mkulu wansembe otumikira mkati mwa kachisi inali yopangidwanso ndi lamadzi, lofiirira, komanso lofiira ndi bafuta wa thonje losansitsa.

Nanga kodi mitundu imeneyi ikutanthauza chiani? Nsaru lamadzi likutanthauza ubatizo wa Yesu Kristu. Kunalembedwa mu 1 Petro 3:21, “Cimenenso cifaniziro cace cikupulumutsani tsopano ndico ubatizo.” Petro akuchitira umboni apa mu 1 Petro 3:21 kuti Yesu anabatizidwa kulandira machimo a dziko, ndipo kuti ubatizowu unali chitsimikizo cha chipulumutso chathu komanso chitetezero cha machimo athu. Chidziwitso choti machimo athu anaperekedwa pa Yesu chikupezeka mu ubatizo Wake (Mateyu 3:15). Monga m’mene nsaru lamadzi linali lofunika kukutira pa chipata cha bwalo la kachisi, choncho ubatizo wa Yesu ndi ofunikanso ku chipulumutso chathu.

Nsaru lofiira, kumbali inayi, ikutanthauza mwazi wa Yesu, pamene nsaru lofiirira ikutanthauza kuti Yesu ndi Mfumu ya ma fumu komanso Mulungu Mwini. Kupeza kufunika kwa nsaru zitatuzi ndikofunika kwa ife kuti tipeze chipulumutso chathu pokhulupilira mwa Yesu. Chobvala chomwe mkulu wansembe ankabvala pamene ankatumikira nsembe chinkatchedwa kuti efodi. Chobvalachi chinalinso ndi mtundu wa lamadzi. Ndipo mkulu wansembe ankabvala mkuzi pamutu pake, ndipo golidi wa phanthiphanthi woona ankaikidwa pa nduwira. Mkuzi omwe unkagwiritsidwa ntchito kugwira golidiyu pa nduwira unalinso wa madzi. Ndipo chingwecho chinalembedwa kuti: “KUPATULIKIRA YEHOVA.”Choondi Chotchulidwa Ndi Nsaru Lamadzi


Kodi choona chotchulidwa ndi nsaru lamadzili ndi chiani tsopano? Kuti tipeze yankho, tiyeni tibwerere ku Baibulo. Mwambiri, pamene tikuganiza za mtundu wamadzi, kawiri kawiri timaganiza za kumwamba, ndipo choncho timaganiza kuti mtundu wamadzi umatanthauza Atate wathu wa kumwamba. Koma kodi Baibulo kimanena chiani pa za mtundu wamadzi? Pa lamadzi, lofiirira, komanso lofiira ndi bafuta wa thonje losansitsa apa, muyenera kuzindikira kuti nsaru lamadzi likutanthauza ubatizo omwe Yesu analandira kwa Yohane Mbatizi m’Chipangano Chatsopano. Zikutanthauza kuti Yesu anabatizidwa kusenza machimo onse a dziko, ndipo kudzera mu ubatizowu Iye indedi anasenza machimo onse a dziko (Mateyu 3:15). Kukanakhala kuti Yesu sanasenze machimo a ali yense mwakubatizidwa, ndiye kuti palibe m’modzi wa ife okhulupilira ake amene tikanabvala kupatulika pamaso pa Mulungu. Ichi ndi chifukwa chake Iye anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi mu mtsinje wa Yordano kutenga machimo onse a anthu, ndipo ichi ndi chifukwa chake Iye anapita pamtanda.

Kunena kuti Mulungu analola chipata cha bwalo la kachisi kukutidwa ndi nsaru lamadzi zikutanthauza ubatizo wa Yesu, ndipo nsaru lofiira likutanthauza kukhetsa kwa mwazi Wake. Nsaru lofiirira likutanthauza Mzimu Woyera, kutsimikiza kuti Yesu ndi Mfumu ya mafumu komanso Mulungu Mwaini. Nsaru lofiira likuloza kuti Yesu Kristu atabatizidwa, anakhetsa mwazi Wake pamtanda kulipira mphotho ya uchimo. Nsaru zimenezi zikupanga Uthenga Wabwino wa choonadi kuti Yesu Mulungu wa choonadi anadza pa dziko lino mu thupi, kusenza machimo a ochimwa ali yense pa thupi Lake, ndipo iye anadzipereka yekha ngati nsembe kukhetsa mwazi Wake. Motere, chihema cha Chipangano Chakale chabvumbulutsa Uthenga Wabwino wa choonadi momveka bwino, kutiuza ife kuti Yesu anachotsa machimo onse a dziko kudzera mu ubatizo Wake. 

Zipilala za chihema zonse zinali zopangidwa ndi matabwa a mtengo wa sitimu, ndipo pansi pake panali mitsukwa ya mkuwa. Ndipo pamwamba panali makamwa a siliva omwe anapangidwa kutchinga matabwawo. Ochimwa ali yense ayenera kuweruzidwa kamba ka machimo ake. Izi ziri chonchi chifukwa mphotho ya uchimo ndi imfa. Munthu ayenera kuweruzidwa kamozi ndi Mulungu ndi munthu ayenera kubwerera ku moyo mwakupeza chisomo cha Mulungu. Nsaru lamadzi la chipulumutso m’Chipangano Chakale ikutsimikidza ubatizo wa Yesu m’Chipangano Chakale, ndipo kudzera mu ubatizowu Yesu Kristu anasenza machimo athu onse. Kenako Iye anasenza chilango cha machimowo mwa kukhetsa mwazi Wake pamtanda, ndipo monga Mfumu ya mafumu komanso Mulungu Mwini, Iye wapulumutsa ife tonse okhulupilira ake mwakupanga chitetezero cha machimo athu onse.

Choncho ubatizo wa Yesu ndi njira yomwe Ambuye wathu anasenzera machimo aonse a ali yense mu dziko lino pofuna kupulumutsa ife ochimwa. Kunali kusenza machimo athu onse pomwe Yesu anabatizidwa, ndipo ubatizo Wake ukulankhula zoonadi mwa tsatane tsatane: Mulungu Mwini anasandulika munthu, anabatizidwa kutenga machimo a munthu ali yense ochimwa, Iye anapachikidwa kukhetsa mwazi Wake pamtanda mpaka kufa m’malo mwa ochimwa, ndipo motero wakhala Ambuye wa chipulumutso choonadi kwa onse okhulupilira mu choonadichi. Kudzera pa chipata cha bwalo la kachisi ndi mitundu yake, Mulungu akupanga kumvetsetsa kwa ife kuti Yesu wakhala Mpulumutsi wa ochimwa onse komanso Ambuye wa Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo.

Bafuta wa thonje losansitsa, kumbali inayi, akutsimikidza Mau a Mulungu, kutiuza ife kuti Ambuye wapulumutsa ife machimo athu onse mwa tsatane tsatane kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi Wake monga Mulungu wathu. Pa bafuta wa thonje losansitsa, nsaru lamadzi, lofiirira, komanso lofiira zinasokedwa kupanga chipata cha bwalo la kachisi. Izi zikuonetsa momveka bwino choonadi cha chipulumutso chopezeka mu ubatizo Yesu, mwazi Wake, komanso umulungu Wake momwe muli chitetezero cha machimo. Choonadichi ndi chinthu chofunika kwambiri mu ntchito ya chipulumutso.

Kuchokera ku kachisiyu komanso ku nsaru lamadzi, lofiirira, komanso lofiira zogwiritsidwa ntchito kupanga chipata komanso chitseko, tingathe kuona kuti Yesu Khristu sanatipulumutse ife mu njira ili yonse, koma kuti, monga Mulungu Mwini, Iye wapulumutsa ife mwa kubatizidwa, kukhetsa mwazi Wake pamtanda mpaka kufa, ndi kuuka kwa akufa. Iye anapulumutsa ife tonse amene takhulupilira molimba mu chili chonse cha Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo osindikizidwa ndi nsaru lamadzi, lofiirira, komanso lofiira.

Kodi n’chifukwa chiani nambala ya zipilala za kachisi zinali nde nde nde 60? Nambala ya chisanu ndi chimodzi imatanthauza munthu. Buku la chibvumbulutso latchula 666, ndipo likunena kuti wanzeru adziwa chobisika cha nambalayi. Nambala ya chitatu ndi nambala ya utatu wa Mulungu. Choncho, nambala 666 ikutanthauza kuyesa kwa munthu kufanana ndi Mulungu. Kodi chokhumba cha ali yense ndi chiani? Kodi sikufuna kukhala monga mulungu? Ndi chifukwa chake satana anabvundura mwano wa munthu, kuti anthu adziyesera kukhala milungu kudzera mu mphamvu zao, m’malo mobadwa mwatsopano ndi kukhala ana a Mulungu mwakukhulupilira mwa Yesu. Kuyesa kubadwa mwatsopano kudzera mu zochitika za munthu ndi kuyesa koipa pamaso pa Mulungu.Mkhate Wamkuwa pa Kachisi Unali Nthunzi wa Ubatizo wa Yesu wa Chipangano Chatsopano


Mkhate unapangidwanso ndi mkuwa. Mkuwa ukutanthauza kuti Yesu anasenza machimo athu onse ndikunyamula kale chiweruzo chathu chonse. Mulungu akutiuza ife kudzera mu mkhate wa mkuwa kuti Iye anatipulumutsa kale ife mwa ngwiro ndikutitsuka kotheratu ndi nsaru lamadzi, lofiirira, komanso lofiira komanso bafuta wa thonje losansitsa. Mwanjira ina, mkhate wa mkuwa ukutanthauza Mau a Uthenga Wabwino otsimikiza chipulumutso cha chitetezero cha machimo, kutiuza ife kuti tapulumutsidwa ku machimo athu a masiku onse. Ukutiuza ife za m’mene machimo athu amasiku onse anatsukidwira. Kwalembedwa monga nthunzi wa choonadi cheni cheni, mkhate wa mkuwa ukutanthauza kuti machimo athu a amasiku onse atsukidwa pokhulupilira mu Mau a ubatizo wa Yesu, pamene guwa la nmsembe likutanthauza chiweruzo cha uchimo.

Madzi a ubatizo wa Yesu akutsimikizidwa ndi mtundu wa lamadzi, kulozera ku ubatizo omwe Yesu analandira kwa Yohane Mbatizi (Mateyu 3:15; 1 Yohane 5:5-10), omwe ukuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chipulumutso komanso chitetezero cha machimo athu. Pamene tibvundukura pa 1 Yohane 5, m’Chipangano Chatsopano, tikuona mtumwi Yohane akunena kuti, “Ndipo ici ndi cilako tililaka naco dziko lapansi, ndico cikhulupiliro cathu.” Ndipo tikuonanso iye akunena kuti ali yense wakhulupilira mwa Mwana ali ndi chitsimikizo cha chikhulupiliro, ndipo kuti madzi, mwazi ndi Mzimu ndi chitsimikizo chikuchitira umboni wa chikhulupiliro chake mwa Mwana. Mulungu tsopano walola ife kulowa mu kachisi pokhulupilira mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, kuti tikhale moyo wathu wa chikhulupiliro m’menemo, kudya pa Mau Ake ndi kupemphera kwa Iye, kubvala chisomo Chake, ndi kukhala tsiku ndi tsiku monga anthu olungama. Mulungu akunena kuti kukhala monga anthu Ake kukutanthauza kupeza chipulumutso pokhulupilira m’Mau a madzi, mwazi, ndi Mzimu, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, ndi kukhala mkati mwa kachisi. 

Akristu ambiri masiku ano akunena kuti zonsezi ndi zopanda nzeru ndipo zili zonse zili bwino bola ngati inu mukukhupilira mwa Yesu, koma ngati mukukhulupilira mwa Yesu mwakhungu popanda Mau Ake a nsaru lamadzi, lofiirira komanso lofiira, ndiye kuti chikhulupiliro chanu ndi chikhulupiliro chabodza. Mwazonse, kodi Akristu osocherawa alibe tchimo m’mitima yao ngakhale kuti amakhulupilira mwa Yesu? Chikhulupiliro chao ndi chakuti iwo sakhulupilira m’Mau a Mulungu monga m’mene alili koma kunyalanyaza kulandira choonadi cha kusinthidwa chonena kuti Yesu anadza pa dziko lino ndi kupulumutsa ochimwa onse ku machimo ao kudzera mu chipulumutso cha madzi ndi mwazi, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo.

Choncho tsopano, ganizani kuti mwafunsa wina wake za munthu wina, ndipo munthu ameneyu, ngakhale iye sakudziwa chili chonse cha munthuyo, akunena kwa inu pongofuna kukutsimikizirani, “munthu ameneyo ndi okhulupirika. Sindinakumanepo naye, koma ndikukutsimikizira kuti munthu ameneyo ndi wa pamwamba.” Kodi mungakhale omasuka pa chitsimikizo chimenechi? Mwachidziwikire zingatheke, koma ngati chikhulupiliro chanu mwa Yesu ndi chokhudzidwa, ichi sichikhulupiliro chomwe Mulungu akufuna kwa inu. Chikhulupiliro chomwe Mulungu akufuna kwa inu ndi chikhulupiliro choikidwa mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, mu Mau oyankhulidwa mwa Mulungu omwe Yesu wapulumutsa ochimwa onse kudzera mu nsaru lamadzi (ubatizo wa Yesu), lofiirira (Mfumu ya mafumu), komanso lofiira (mwazi wa Yesu). Musanakhulupilire mwa Yesu, muyenera kudziwa bwino bwino kudzera mu zomwe Uthenga Wabwino wa Ambuye wapulumutsa inu.

Tikanena kuti timakhulupilira mwa Yesu, tiyenera kukhala ndi kumvetsetsa za m’mene Iye anatipulumutsira ife ku machimo kudzera mu madzi (ubatizo wa Yesu), mwazi wake (imfa ya Yesu), ndi Mzimu (umulungu wa Yesu). Kaya chikhulupiliro chanu chinapangidwa mwa ngwiro kapena ai podalira kaya podziwa Uthenga Wabwino umenewu wachitetezero cha machimo kapena ai. Chikhulupiliro chanu ndi choonadi ngati m’makhulupilira ngati Mpulumutsi wanu podalira umboni wa Mau a chipulumutso, ubatizo ndi mwazi wa Yesu momwe muli Uthenga Wabwino wa choonadi wa chikhululukiro cha machimo.Chikhulupiliro Chomwe Chimanyoza Yesu


Kodi ndi chikhulupiliro chotani, tsopano, chomwe chimanyoza Yesu? Tiyeni tifufuze. 

Muyenera kuzindikira apa kuti kukhulupilira mwa Yesu mwa khungu kumangonyoza Yesu amene ndi Mulungu Mwini. Anthu ena amanena kwa Ambuye, “zinali zondibvuta kukhulupilira mwa inu, koma chifukwa chakuti Inu mwanena kuti ndinu Mwana wa Mulungu komanso Mulungu Mwini, ndidzakhulupilira mwa Inu monga kukonda.” Ichi, okondedwa okhulupilira anzanga ndi chikhulupiliro chonyoza Yesu Mpulumutsi. Anthu onse otere ayenera kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake omwe muli Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo. Kukhulupilira mwa Yesu popnda kudziwa Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo ndi kunyoza kwakukuru kwa Ambuye koposa bola osakhulupilira mwa Iye. Kulalikira Uthenga pongokhulupilira mu mwazi wa Yesu ndi chimodzi modzi kuyesa kuyendetsa galimoto popanda kudziwa komwe kuli chiongolero. Muyenera kuzindikira apa kuti kuuza chabe anthu kuti akhulupilire mwa Yesu ndi kunyozanso Mulungu. Yesu sakufuna chikhulupiliro chakhungu kwa inu; koma, Iye akufuna inu kuti mukhulupilire mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo. 

Pamene mukukhulupilira mwa Yesu muyenera kukhulupilira kuti Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo ndi unapangidwa ndi ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Ndipo pamene inu mwakhulupilira mwa Yesu, muyenera kudziwa Uthenga Wabwinowu wa chitetezero mwatsatane tsatane podalira pa Mau a Mulungu, kuzindikira m’mene Iye anapangira chitetezero cha machimo anu ndi kupulumutsa inu, ndipo kenako kukhulupilira m’Mau amenewa. Pamene muli ndi kumvetsetsa koyenera pa za m’mene Yesu anakupulumutsirani inu kudzera m’Mau, ndi kudziwa komanso kukhulupilira mu chikhadzikitso cha Mau a Mulungu a nsaru lamadzi, lofiirira komanso lofiira omwe akupulumutsani inu-ndi pokhapo pamene chikhulupiliro chanu chili choonadi, ndipo ichi ndi chikhulupiliro chosasintha kwamuyaya chomwe chabweretsa chikhululukiro cha machimo kwa inu.Simungabadwe Mwatsopano Pokha Pokha Inu Ngati Mwakhulupilira Mwa Ambuye, Chikhazikitso Cheni Cheni Cha Nsaru Lamadzi, Lofiirira, Komanso Lofiira


Ambuye wathu anapulumutsa inu ndi ine. Pamene ndikuona chipulumutso chimenechi kudzera mu kachisi wa Mulungu, mau sangafotokoze chiyamiko chomwe ndili nacho kuti Iye anatipulumutsa ife molimba kudzera mu nsaru lamadzi, lofiirira, komanso lofiira, komanso kuthokoza komwe ndiri nako kuti Iye anatipatsa ife chikhulupiliro kuti tikhupilire mu choonadi chobvumbulitsdwa mu nsaru lamadzi, lofiirira komanso lofiira, Mau a Uthenga Wabwino a chitetezero cha machimo. Mwachiyamiko ndikulemekeza Mulungu!

Ngakhale mkulu wansembe sankalowa m’malo oyera pokha pokha iye choyamba apeze chikhululukiro cha machimo ake pa guwa la nsembe. Momwemonso, ndizosatheka kwa ochimwa ali yense kulowa m’malo oyera ngati sanavale chisomo cha Mulungu komanso kulandira chikhululukiro cha machimo ake. Kodi munthu amene sanachotseredwe machimo ake onse angatsegule khomo la malo oyera ndi kulowa mkati? Ai, nzosatheka. Ngati muthu wotere angalowe m’malo oyera a Mulungu, iye adzafa mwachidziwikire. Kutali kudalitsidwa, iye adzatembereredwa ndi kunena kuti, “n’chifukwa chiani muli mdima muno? sindikuona chilichonse! Pamene ndinali panja pa malo opatulika, ndimaona chinachake ngakhale chinali chosokonezeka, koma tsopano sindikuona chilichonse!” Palibe ochimwa amene angalowe m’malo oyera ndikukhala m’menemo.

Kudzera mu chobisika cha chipulumutso chobisidwa mu mitundu inayi ya nsaru zogwiritsidwa ntchito kupanga chitseko cha kachisi, Ambuye wathu wapulumutsa ife mwangwiro. Ndi nsaru lamadzi, lofiirira, ndi lofiira, komanso ndi bafuta wa thonje losansitsa, Mulungu walankhula choonadi kwa ife kudzera mu tsatanetsatane wa Mau ake olimba a lonjezo omwe walola ife kubadwanso mwatsopano ndi kupulumutsa ife. 

Okondedwa okhulupilira anzanga, kodi tonse tinapulumutsidwa bwanji? Tinapulumutsidwa mu njira ili yonse? Ai, si choncho. Pokha pokha ngati mwakhulupilira m’Mau a nsaru lamadzi, lofiirira, komanso lofiira, simungamvetsetse Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo kapena kupeza chipulumutso chanu ku uchimo. Nsaru lamadzi silitanthauza Mulungu. Limatanthauza ubatizo wa Yesu. Likutsimikiza ubatizo omwe Yesu analandira, madzi omwe Ambuye anasenzera machimo onse a ochimwa ali yense mu dziko lino pa thupi Lake (Mateyu 3:15).

Mungafike pa guwa la nsembe ngakhale simunakhulupilire mu nsaru lamadzi. Koma simungatsegure khomo la chihema momwe Mulungu amakhala ndi kulowa mkati. Simungangolowa m’menemo. Ndi chifukwa chake pamene mwakhulupilira mwa Yesu, muyenera kukhulupilira mu nsaru lamadzi (ubatizo omwe Yesu analandira), nsaru lofiira (mwazi omwe Yesu anakhetsa pamtanda) komanso nsaru lofiirira (Yesu ndi Mwana wa Mulungu komanso Mulungu Mwini). Pokhapo pamene mwakhulupilira mu zinthu zitatu zonsezi mungakhale ndi chikhulupiliro chobvomerezeka ndi Mulungu. Pokha pokha ngati mwakhulupilira mu zinthu zitatu zimenezi, simungalowe pa khomo la malo oyera momwe Mulungu amakhala.

Akristu ambiri amaganiza kuti pamene iwo alowa kudzera pa chipata cha bwalo la kachisi, adzapulumutsidwa, koma ichi sichipulumutso. Kodi muyenera kulowera kuti kuti mupulumutsidwe? Pokhapo ngati mwalowa m’malo oyera, malo okhala Mulungu, mudzapeza chipulumutso chanu. Kuti mulowe m’malo oyera a Mulungu, muyenera kudutsa pa mkhate wamkuwa popanda kulephera. Mkhate wamkuwa umatsimikiza ubatizo wa Yesu, ndipo mungalowe m’malo oyera a Mulungu pokhapo ngati mwadzitsuka nokha posambitsa machimo anu amasiku onse ndi ubatizo wa Yesu, monga ansembe a Chipangano Chakale sankalowa m’malo oyera pokhapo ngati iwo asamba okha pa mkhate wamkuwa. Ndi chifukwa chake Yesu anasambitsa mapazi a ophunzira Ake: pakuti kunali kwa ife kuti tikumbukire kuti Iye anatsuka kale ndi kupulumutsa ife ku machimo athu onse a masiku onse ndi ubatizo Wake.

Lamulo la Mulungu likunena kuti, “Pakuti mphotho yace ya ucimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiye moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu” (Aroma 6:23). Mulungu ayenera kuweruza machimo a munthu popanda kulephera, koma Iye anapereka machimo onse kwa Mwana Wake Yesu ndi kuweruza Mwana Wake m’malo mwathu. Umu ndi m’mene Mulungu anatipulumutsira ife. Ichi ndi chikondi cha Mulungu, ndipo ndi njira ya Mulungu yopulumutsira ife. Chipulumutso choonadi chimapezeka kudzera muchikhulupiliro, pokhulupilira mu ubatizo wa Yesu, mwazi Wake, imfa komanso kuuka Kwake, zomwe pamodzi zikupanga Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo.Kubadwa Mwatsopano, Simuyenera Kunyalanyaza Uthenga Wabwino wa Chitetezero Cha Machimo Omwe Walembedwa mu Baibulo


Sindimatsutsa maganizo a munthu mophweka. Nthawi zonse pamene wina wake akukamba kwa ine pa china chake chomwe sindikuchidziwa bwino, ndimamvetsera mwatcheru, kubvomereza nzeru zanga zochepa mu mkhaniyo, ndi kupempha iye kuti andiphunzitse. Mwachisanzo pamene ndinkaphunzira za kachisi, ndinafufuza zolemba zochuluka. Koma sindinapeze kukhutitsdwa kuli konse pa yankho la mafunso anga.

Kodi ndinayenera kubwerera kuti tsopano? Ndinayenera kubwerera mu Baibulo. Kodi nanga, ndipati mu Baibulo pamene Mulungu akulankhula za kachisi? Iye akulankhula zimenezi mwatsatane tsatane Buku la Eksodo. Choncho zinali pamene ndinkawerenga Buku la Eksodo pomwe ndinazindikira tanthauzo la kachisi kuchokera m’Mau a Mulungu.

Okondedwa okhulupilira anzanga, chifukwa chakuti mwangokhulupilira mwa Yesu mu njira ili yonse, izi sizikutanthauza kuti munapulumutsidwa mopanda malire. Kapena kunena mwakhungu kuti mwabadwanso mwatsopano chifukwa chakuti mumapita kukachisi. A Yuda onse ankakhulupilira mwa Mulungu moyenera, ndipo Nikodemo sizinali zodabwitsa. Koma Ambuye wathu ananena kwa iye molimba mu Yohane 3, “ndiwe mphunzitsi wa Ayuda koma kodi sudziwa zimenezi? Palibe angaone kapena kulowa Ufumu wa Mulungu pokha pokha iye abadwe mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.”

Ali yense amene amakhulupilira mwa Yesu ayenera kukhulupilira mu nsaru lamadzi (kuti Yesu anasenza tchimo lathu lili lonse kamodzi kokha pamene Iye anabatizidwa), nsaru lofiira (kuti Yesu anafa kamba ka machimo athu), komanso nsaru lofiirira (kuti Yesu ndi Mpulumutsi, Mwana wa Mulungu, komanso Mulungu Mwini); ndipo ali yense ayenera kukhulupilira kuti Yesu ndi Mpulumutsi wa ochimwa onse. Ali yense amene sakhulupilira mu choonadichi sanabadwe mwatsopano ngakhale kuti munthu ameneyo akukhulupilira mwa Yesu, ndipo nzosatheka kwa munthu ameneyu kulowa m’malo oyera, Ufumu wa Mulungu. Ambuye wathu anakamba momveka bwino kuti a Kristu osochera chotere sangakhale moyo wao wa chikhulupiliro moyenera. Kodi zikanakhala zodabwitsa chotani kukanakhala kuti ali yense anabadwa mwatsopano pongokhulupilira mwa Yesu mwakhungu? Ali yense bwenzi akuyimba chiyamiko kwa Ambuye popeza chikhulupiliro mosabvuta. Koma izi si m’mene zilili; mwa kusemphana kwake, anthu ambiri amakhulupilira mwa Yesu popanda kubadwa mwatsopano.

Zikabwera kukhulupilira mwa Yesu, muyenera kudziwa choonadi cheni cheni cha mu Baibulo. Baibulo likunena momveka bwino kuti inu muyenera kudziwa moyenera ndi kukhulupilira mu Uthenga Wabwino wa nsaru lamadzi, lofiira komanso lofiirira, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, ndipo pokhapo mungalowe m’malo oyera ndi kukhala pamodzi ndi Mulungu. Moyo wanu udzaunikiridwa ndi nyali ya golidi, muzadzadza ndi chakudya cha uzimu kuchokera ku gome la mkate woonekeratu, mudzakhala ndi kuthekera kopemphera kwa Mulungu malingana ndi chifuniro chake pa guwa lofukizapo, mudzapita kumwamba pamene mulungu waitana inu. Komangati inu mukukhulupilira mwa Yesu mwa umbuli, ndiye kuti izi zikutanthauza kuti simunakhulupilire mwa Yesu.Ambuye Watsuka Machimo Anu Onse Ndi Nsaru Lamadzi


M’maganizo mwanu, zingaoneka ngati simungapange cholakwika koma kuchita chili chonse mopanda bvuto. Koma pamene mwayamba kuchita china chake, kulephera kwa luso lanu komanso zolakwa zanu zimaonekera kuti ali yense azione. Tonse ndife odzadza ndi zolakwika, ndipo palibe wina wa ife amene angapewe kuchita tchimo. Koma ngakhale zili choncho, ndi nsaru lamadzi, lofiirira, komanso lofiira, Ambuye wapulumutsa ife kudzera mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, ndipo choncho tingalowe m’malo oyera a Mulungu mwa chikhulupiliro. Kukanakhala kuti Mulungu sanatipulumutse ife kudzera mu nsaru lamadzi, lofiirira komanso lofiira, ngati Iye sakanabweretsa chipulumutso mwa njira imeneyi, ndiye kuti palibe m’modzi waife amene tikanalowa m’malo oyera. Zikanakhala zosatheka ngakhale tikanakhala ndi chikhulupiliro cholimba motani. Chifukwa chiani? Chifukwa chakuti palibe ali yense amene angalowe m’malo oyera ngati kukhanakhala kodalira zikhulupiliro za munthu m’malo mwa chikhulupiliro choperekedwa ndi Mulungu. Kuonjezerapo anthu otere akanakhala anthu ochimwa kwambiri kupatula kukhulupilira kwao mwa Yesu. 

Komabe, Yesu wapulumutsa ochimwa operewera chotere ngati ife kudzera mwa nsaru lamadzi, lofiirira komanso lofiira ndi bafuta wa thonje losansitsa, kudzera muchikonzero cha chipulumutso Chake komanso Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo. Iye wachotsa machimo athu onse. Kodi mukukhulupilira mu zimenezi? Kodi muli ndi Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo komanso umboni Wake mu mtima mwanu? Pokhapo pamene muli ndi umboni wa Mau mungabvale pamutu panu golidi ya mphanthimphanthi yonena kuti, “KUPATULIKIRA AMBUYE.” Ndipo pokhapo mungagwire ntchito ya unsembe ndi kunena kwa anthu molimba mtima kuti ndinu mtumiki wa Mulungu otumikira ngati wa nsembe.

Goldi wa mphanthimphanthi ankaikidwa pa nduwira yobvalidwa ndi mkulu wa nsembe patsogolo pamutu wake, ndipo golidi wa mphanthimphanthiyu ankaikidwa ndi mkuzi wamadzi. Kodi ndi chifukwa chiani mkuzi wamadzi unkagwiritsidwa ntchito kuika golidiyu? Ndi chifukwa chakuti pamene Ambuye wathu anapulumutsa ife kudzera mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, Iye anasenza machimo athu ndi kupanga ife olungama kudzera mu ubatizo Wake (kufanana kwa kuika manja m’Chipangano Chakale). Posatengera chikhulupiliro chanu mwa Yesu, chinsinsi chopeza chiyero cha Ambuye chikupezeka m’Mau obisikawa a nsaru lamadzi, lofiirira komanso lofiira, m’Mau a chipulumutso.

Kodi tinakhala bwanji anthu olungama? Pamene Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi, Iye anati kwa Yohane, “Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero” (Mateyu 3:15). Yesu anapulumutsa ife tonse ku machimo athu mwakubatizidwa, ndipo chifukwa Yesu anasenza machimo athu kudzera mu ubatizowu, onse a ife amene takhulupilira mwa izi takhala tsopano anthu olungama. Kukanakhala kuti Yesu sanabatizidwe, kodi tikananena bwanji kuti ndife anthu opanda tchimo? Popanda ubatizo wa Yesu, palibe tchimo lathu lomwe likanachotsedwa pa machimo onse, ngakhale tikanakhulupilira chotani mwa Yesu komanso kulila chotani pakuganizira masautso ndi imfa Yake pamtanda. Kulibe misozi yomwe tingakhetse pa masautso a Yesu yomwe ingachotse tchimo lili lonse.

Kunalembedwa pa golide wa mphanthimphanthi wa mkulu wansembe, “KUPATULIKIRA AMBUYE.” Lemba ili lakwaniritsidwa mu mitima mwathu. Chifukwa Yesu anachotsa machimo athu kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi, chifukwa Ambuye Mulungu anabvala mphulupulu zathu kwa Iye, ndipo chifukwa machimo athu onse anaperekedwaldi pa Yesu, posatengera zolakwa za machitidwe athu, takhala anthu olungama mwachikhulupiliro ndipo tingayandikire Mulungu molimba mtima, pakuti Mau a chipulumutso alembedwa apa mu Baibulo monga Mau a Mulungu. Ndipo monga anthu olungama chotere, tingakhale mwa chikhulupiliro ndikulalika chikhulupiliro cholungamachi kwa ali yense. 

Akristu amayimba mwakhungu, “♪ ndapulumutsidwa; ♪ mwapulumutsidwa; ♪ tonse tapulumutsidwa. ♪” koma mopanda njira ili yonse chipulumutsochi chadza kwa mu Kristu ali yense amene akukhulupilira mwa Yesu muli monse momwe iye wafunira. Pokha pokha ngati munthu ali ndi Mau a Uthenga Wabwino a chitetezero cha machimo mu mtima mwake, munthuyu sanapulumutsidwe. Sizitengera kuti munthu akukhulupilira motani mwa Yesu; ngati zonse ndi zochita zake, ndiye kuti iye sanapulumutsidwe. Ndi zopanda ntchito popeza akukonda Mulungu mwa iye yekha popanda kukondedwa ndi Mulungu. Ngati simukhulupilira mu zonse ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, ndiye kuti chikondi chonse ndi masautso onse omwe muli nao pamaso pa Ambuye zili chabe ndipo sizizayankhidwa.

Akristu Ambiri lero atenga chipulumutso mophweka moti iwo amaganiza kuti chingapezeke mwanjira ili yonse yomwe iwo asankha, monga pali njira zambiri za chipulumutso. Koma izi zingatheke bwanji? Kodi kungakhale bwanji njira zambiri zosiyana za chipulumutso? Pali njira imodzi ya chipulumutso chamuyaya, ndipo njirayi ndi Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu. Zina zonse ndi zongobweretsa imfa kumapeto. Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu ndi omwe mukufunika kuti mupulumutsidwe pamaso pa Mulungu; chili chonse ndi chopanda ntchito.Chinsinsi Cha Chipulumutso Chobvumbulitsidwa mu Nsaru Lamadzi Lakachisi


Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, Uthenga Wabwino wa nsaru lamadzi, lofiirira komanso lofiira, ndi mphatso ya Mulungu ya chipulumutso kwa ife. Ndi mphatso imeneyi ya chipulumutso yomwe yalola ife kulowa m’malo opatulika ndi kukhala m’menemo yatipanaga ife kukhala anthu olungama. Potipanga ife kukhala anthu olungama, iyo yatisogolera ife mkachisi kuti tikhale m’menemo ndi kudya mkate wa uzimu, Mau a Mulungu. Ndipo nthawi zonse taimilira pa mpando wachifundo wa Mulungu ndi kupemphera kwa Iye, yatidalitsa ife ndi chisomo choperekedwa ndi Mulungu. Ndi chifukwa chake chipulumutso ndi chamtengo wapamwamba.

Yesu wauza ife kuti timange nyumba zathu pathanthwe. Thanthweli ndilosaposa chipulumutso chathu, chomwe chinakwaniritsidwa ndi machitidwe olungama a Yesu, ndiko kuti, ubatizo Wake ndi mwazi. Choncho tsopano, tiyeni tonse tipulumutsidwe kuti tikhala ndi chikhulupiliro chathu, kukhala ana a Mulungu, kulowa Ufumu wa kumwamba, ndi kusangalala moyo wosatha. Chifukwa talandira Uthenga Wabwino wa nsaru lamadzi, lofiirira, komanso lofiira ndi bafuta wa thonje losansitsa, Uthenga Wabwino wa Yesu wa chitetezero cha machimo, tingalowe tsopano m’malo oyera mwa chikhulupiliro chimenechi. Ngakhale tisanapulumutsidwe, Yesu anasenza machimo athu kudzera mu ubatizo Wake ndipo Iye anaweruzidwa pamtanda, ndipo ndi chifukwa chake tapeza chipulumutso pokhulupilira mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo.

Ubatizo omwe Yesu analandira ndi mwazi Wake omwe anakhetsa kupanga chitetezero cha machimo onse zikupanga Uthenga Wabwino omwe watsuka machimo anu onse. Kodi mukukhulupilira mu Uthenga Wabwinowu tsopano? Uthenga Wabwino wa choonadi ndi Uthenga Wabwino wa kumwamba wa chitetezero cha machimo omwe watsuka ngakhale machimo anu a masiku onse. Mwapulumutsidwa ndi kubadwa mwatsopano pokhulupilira mu Uthenga Wabwinowu wachikhululukiro cha machimo. Ambuye wapulumutsa ife kudzera mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo omwe wafufuta tchimo lili lonse la machimo athu a masiku onse.

Ndikuthokoza Ambuye pa Mau Ake. Aleluya! Chiyamiko kwa Ambuye.

 Mulungu akudalitseni nonse!