Sermons

【3-17】<1 Yohane 5:4-9> Uthenga Wabwino Wakale Omwe Ungagonjetse Machimo a Dziko Lapansi<1 Yohane 5:4-9>

Pakuti ciri conse cabadwa mwa Mulungu cililaka dziko lapansi; ndipo ici ndi cilako tililaka naco dziko lapansi, ndico cikhulupiriro cathu. Koma ndani iye wolilaka dziko lapansi, koma iye amene akhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu; Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, ndiye Yesu Kristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi. Ndipo Mzimu ndiye wakucita umboni, cifukwa Mzimu ndiye coonadi. Pakuti pali atatu akucita umboni, Mzimu, ndi madzi, ndi mwazi; ndipo iwo atatu ali mmodzi. Ngati tilandira umboni wa anthu, umboni wa Mulungu uposa; chifukwa umboni wa Mulungu ndi uwu, kuti anacita umboni za Mwana wace.Mulungu anapanga kuthekera kwa inu kuti mugonjetse dziko, kupambana pa uchimo, ndi kugonjetsa mudierekezi kuti tikhale moyo opambana pokhulupilira mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo omwe Yesu anakwaniritsa. Komabe, ngati inu mukhulupilira mwa Yesu posakhulupilira Mau a Uthenga Wabwino wa “madzi” a ubatizo wa Yesu, simungapulumutsidwe ku machimo anu amasiku onse. Ndi chifukwa chake mtumwi Yohane ananena mu 1 Yohane 5:5-10 kuti chikhulupiliro chogonjetsa dziko ndi chikhulupiliro choikidwa m’madzi, mwazi ndi Mzimu. Mulungu Atate anapereka mphotho yonse ya machimo athu kwa Yesu. Yesu anandza pa dziko lino mu thupi la munthu, kulandira machimo onse a mtundu onse wa anthu kudzera mu ubatizo omwe Iye analandira mu mtsinje wa Yordano, kusenza machimo onse a dziko pa thupi Lake, kukhetsa mwazi Wake pamtanda, ndipo motero kulipira mphotho ya machimo onse a mtundu wa anthu ndi ubatizo Wake komanso mwazi.

Kuti Ife tigonjetse dziko lino, tiyenera kukhulupilira mu Uthenga Wabwino wa ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Chikhulupiliro chokha chomwe chingatilore ife kubadwa mwatsopano kuti tigonjetse dziko lino ndi chikhulupiliro choikidwa mu Mau a Uthenga Wabwino okwaniritsidwa ndi ubatizo komanso mwazi Wake, Mpulumutsi wathu weni weni. Ngati inu mwakhulupilira mu Uthenga Wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, ndiye kuti chikhulupiliro chanu chidzabvomereka ndi Mulungu; koma ngati mulibe chikhulupiliro mu Mau Uthenga Wabwinowu  wa ubatizo ndi mwazi wa Yesu, ndiye kuti simunapeze chipulumutso chanu. Zonse ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake ndizofunika ku chitetezero cha machimo onse a dziko omwe Yesu anapanga pa dziko lino, ndipo choncho ngati inu simukhulupilira muchimodzi mwaicho, ndiye  kuti kutali ndi kupulumutsidwa ku machimo onse a dziko, inu mudzathera kuchionongeko. Ndi chifukwa chake tikutcha Uthenga Wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pamtanda ngati Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo. Pafupi fupi Akristu onse amakhulupilira mwa mtanda wa Yesu okha, koma kuti inu mubadwedi mwatsopano, chikhulupiliro mu ubatizo wa Yesu pomwe analandira kwa Yohane Mbatizi ndi ofunikanso kwa inu.Pokha Pokha Mukhale Ndi Uthenga Wabwino wa Chitetezero Cha Machimo Okwaniritsidwa Ndi Yesu, Simungapulumutsidwe ku Uchimo


Ndikudziwa kuti pali Akristu ambiri opembedza ozungulira dziko lapansi. Ena a iwo ali  odzipereka kuphedwa chifukwa cha chikhulupiliro chao, pamene ena zomwe iwo amaganiza ndi Chikristu cha moyo wakudzipereka, kupemphera mapemphero akulapa tsiku ndi tsiku komanso kupereka nthawi yao yonse yaulere kuzinthu za bwino, kuganiza mwa iwo okha, “ndapereka chuma changa chonse kwa Mulungu ndikukhuthula moyo wanga onse kwa Iye. Sindinakwatire kuti nditumikire Ambuye. Choncho ndiri ndichidaliro kuti Mulungu sadzandikana ine.” Koma Akristu otere adakali ndi machimo mu mitima yao, koma iwo akudalirabe chipulumutso chao, kuganiza kuti, “ndikukhulupilira kuti Yesu anadza pa dziko lino monga munthu ndi kufa pamtanda kupulumutsa ine. Choncho chifukwa chakuti ndiri ndi machimo ochepa okha mu mtima mwanga, kodi Mulungu angandipereke kugahena?” komabe, anthu otere sanabadwe mwatsopano, ndipo choncho onse adzaponyedwa kugahena pamapeto pake.

Komabe ena amanena kuti popeza Yesu Kristu anadza pa dziko lino mwakubadwa ndi Mzimu Woyera ndikusenza chilango chonse cha machimo a mtundu onse wa anthu ndikupachikidwa Kwake, munthu sadzaweruzidwa kamba ka machimo ake. Koma machimo anu angachoke bwanji pokha pokha ngati mwakhulupilira kuti Yesu anasenza onse kudzera mu ubatizo Wake? Motero kukhulupilira mu mtanda okha ndi kukhulupilira mwa Yesu malingana ndi kufuna kwanu. Ndi chikhulupiliro cholakwika chomwe chamangidwa pa maganizo anu. Chikhulupiliro chotere chomwe changoikidwa mu mtanda wa Yesu okha sichikhulupiliro cha ngwiro, koma chopangidwa mwa inu nokha, ndipo choncho kutali ndi kuima mu Buku la obadwa mwatsopano, m’malo mwake mudzapeza chionongeko kumapeto. Kumbukirani izi moyenera. Pobweretsa chikhululukiro cha machimo ndi chipulumutso kwa ife, Ambuye anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi kuti alandire machimo onse a dziko, Iye anaweruzidwa kamba ka machimo ndi kulipira mphotho yake mwakukhetsa mwazi Wake pamtanda m’malo mwathu, ndipo Iye anauka kwa akufa m’masiku atatu. Pokha pokha ngati inu mwadziwa ndi kukhulupilira mu Uthenga Wabwinowu wa chitetezero cha machimo, onena kuti Yesu anasenza machimo onse a mtundu onse wa anthu mwakubatizidwa ndi Yohane Mbatizi mu mtsinje wa Yordano, chikhulupiliro chanu mwa Yesu ndi cholakwika.

Pamapeto pake, ngati simunabvale ubatizo wa Yesu Kristu mwa chikhulupiliro, ndiye kuti chikhulupiliro chanu sichikhulupiliro cha chitetezero cha machimo, kapena simunapulumutsidwe ku machimo anu onse. Yesu Kristu anabadwa pa dziko lino kuchokera mwa Mzimu Woyera chifukwa cha chikhululukiro cha machimo athu, ndipo ndi ubatizo omwe Iye analandira kwa Yohane Mbatizi mu mtsinje wa Yordano komanso mwazi omwe anakhetsa pamtanda, Iye anapanga chitetezero changwiro ku machimo athu onse. Polimbana ndi kugonjetsa satana motero, Kristu wafufuta kotheratu machimo onse a ali yense mu dziko lino, ndipo Iye wabweretsa chipulumutso changwiro cha kusinthidwa kwa okhulupilira Ake onse. Yesu Kristu anachotsa machimo athu onse mwakubatizidwa, kufa pamtanda, kuuka kwa akufa mwa masiku atatu, ndipo tsopano wakhala kudzanja lamanja la mpando wa Mulungu Atate.

Ndi ubatizo Wake komanso mwazi, Yesu wachotsa machimo athu onse ndikukhala Mpulumutsi wa ife tonse amene takhulupilira mwa Ambuye malingana ndi Mau a Uthenga Wabwino akusinthidwa; ndipo polandira Mzimu Woyera mu mitima yathu, Iye tsopano akuchitira umboni pa chipulumutso chathu kunena kuti, “ndakupulumutsani motere, ndipo ndi ubatizo wanga komanso mwazi, ndapanga chitetezero cha machimo anu onse kukhala chipulumutso changwiro. Chikhulupiliro cha chikhululukiro cha machimo chomwe chalola inu kugonjetsa dziko ndi chomwe chaikidwa mu ubatizo wanga komanso mwazi, ndipo monga m’mene ndagonjetsera dziko, inunso mudzaligonjetsa. Ndakupulumutsani ku machimo onse a dziko kudzera mwa madzi anga ndi mwazi. Limbani mtima pakuti mungagonjetse dziko!” mkati mwa ife obadwa mwatsopano, tili ndi Mzimu oyera ochitira umboni chipulumutso chathu.

Uthenga Wabwino omwe ukuchitira umboni wachipulumutso mkati mwa olungama ndi Uthenga Wabwino wa ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Yesu kristu anachotsa machimo onse a dziko mwakubatizidwa. Iye anasenza onse pa thupi Lake. Mulungu wapulumutsa ife mwa chikhulupiliro chathu mu chipulumutso cha machimo athu. Uthenga Wabwino oonadiwu ukunena kuti machimo onse a dziko anaperekedwa pa Yesu Kristu pamene Iye anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi mu mtsinje wa Yordano, kuti Iye anakhetsa mwazi Wake kwa ife pamtanda, ndipo kuti Iye ndi Mulungu Mwini. Ndipo chifukwa Kristu anauka kwa akufa m’masiku atatu, ndipo chifukwa tiri ndi umboni wa Mau a ubatizo ndi mwazi wa Yesu mu mitima yathu, tiri ndi kuthekera kogonjetsa satana, kumenyana ndi kugonjetsa aneneri onyenga, komanso kupilira ndi kupambana pa masautso ndi mazunzo a dziko lapansi. Chikhulupiliro chomwe chimagonjetsa dziko ndi chokhulupilira mu zinthu zitatu izi-ubatizo wa Yesu, mwazi Wake, komanso umulungu Wake monga Mwana wa Mulungu.

Zikomo pa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pamtanda, tingagonjetse satana mwachikhulupiliro ndi kupambana pa dziko lino ndi machimo Ake. Ndi mwa kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pamtanda kuti tingaimilire kulimbana ndi aneneri onyenga ochuluka ndi kuwagonjetsa onse. Uthenga Wabwino wa choonadi wa chikhululukiro  cha machimo ndi opangidwa ndi ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Palibe m’Kristu amene angagonjetse dziko pokha pokha akhale ndi chikhulupiliro m’Mau awa a chitetezero cha machimo.

Nanga inu bwanji? Kodi muli ndi Mau a choonadi a ubatizo ndi mwazi wa Yesu mu mtima mwanu? Kodi muli ndi madzi a ubatizo wa Yesu komanso mwazi Wake? Kodi mumakhulupilira mu Mau a choonadi onena kuti machimo onse a dziko anaperekedwa pa Yesu pamene Iye anabatizidwa? Ndipo kodi mukukhulupilira m’Mau a choonadi onena kuti Yesu Kristu, pamene Iye anabatizidwa, anapachikidwa mpaka kufa m’malo mwathu ndi kusenza chiweruzo chathu chonse? Chikhulupiliro m’Mauwa a ubatizo wa Yesu komanso mwazi Wake pamtanda ndi chikhulupiliro chomwe chalola ife kupambana dziko lino lapansi. 

Mtumwi Yohane anakhulupiliranso anakhulupiliranso mu ubatizo wa Yesu, mwazi Wake, komanso umulungu Wake. Ndichifukwa chake iye anagonjetsa dziko ndi kulalikira komanso  kuphunzitsa Uthenga Wabwino wa choonadiwu wa madzi ndi mwazi, Uthenga Wabwino wa chikhululukiro  cha machimo, kwa abale omwe akukumana ndi masautso komanso mazunzo. Iye anawauza iwo kuti anagonjetsa dziko, pakuti iwo anakhulupilira ndi mtima onse mwa Yesu Kristu amene anadza mwa madzi, mwazi ndi Mzimu. Kodi ndi chikhulupiliro chotani chomwe oyera mtima amagonjetsera dziko? Ndi chikhulupiliro chokhulupilira m’Mau a Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo komanso mwa Yesu Kristu amene anadza mwa madzi, mwazi ndi Mzimu. Izi ndi zomwe mtumwi Yohane analemba m’malembo a ndime yalero.

Kwalembedwa mu 1 Yohane 5:8: “Pakuti pali atatu akucita umboni, Mzimu, ndi madzi, ndi mwazi; ndipo iwo atatu ali m’modzi.” Akristu ambiri amanena kuti amakhulupilira mwa mwazi wa Yesu komanso Mzimu, koma palibe ali yense wa iwo amene akudziwa Mau a “madzi,” kuti Yesu anasenza machimo onse a dziko mwakubatizidwa ndi  Yohane Mbatizi. Mu Baibulo, ubatizo (madzi) wa Yesu ndi ofunuika ku Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo. Choncho mtumwi Petro analemba mu 1 Petro 3:21 kuti ubatizo wa Yesu ndi chifaniziro cha chipulumutso chathu: “Cimenenso cifaniziro cace cikupulumutsani tsopano, ndico ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lace la thupi, komatu funso lace la cikumbumtima cokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Kristu.” 

Pakati pa Akristu osawerengeka amene akhulupilira mwa Yesu koma asiya ubatizo Wake mpaka lero, okhawo amene akana chiphunzitso chabodzachi, atembenuka ndikukhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu monga chipulumutso chao angapulumutsidwe. Ngakhale m’makhulupilira mu mwazi wa Yesu komanso umulungu Wake, ngati simukhulupilira mu “madzi” a ubatizo Wake mpaka kumapeto, ndiye kuti simungakhale munthu olungama kapena kugonjetsa dziko, koma m’malo mwake mudzakhala ochimwa mpaka kumapeto ngakhale mungakhulupilire bwanji mwa Yesu. Simungabadwe mwatsopano chifukwa simunakhulupilire mu ubatizo wa chitetezero cha machimo. Ndi chifukwa chake muyenera kukhulupilira mu chikhululukiro cha machimo, ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, lomwe ndi dzanja la chipulumutso chomwe Ambuye anakupatsani. Ndipo mwachikhulupiliro chimenechi muyenera kulimbana ndi kugonjetsa satana kuti mupeze chipulumutso chanu.

Mau a Mulungu ndi lupanga, moyo komanso kuunika. Ndimakonda kubwereza mfundo imeneyi, koma ngakhale tsopano Akristu ambiri akukhulupilira mu mwazi okha wa Yesu komanso Mzimu; ndipo ngati inu mwakhulupilira mu zinthu ziwiri zokhazi, ndiye kuti m’malo mogonjetsa dziko, mudzagwa ndi  kuonongeka kukwiriridwa pansi pa machimo anu. Ngakhale Mulungu wanena, “dzuka, wala,” Akristu ambiri akulephera kuwalitsa nyali zao popeza iwo wakhulupilira mwa Yesu mwatheka, pokhapo adzaponyedwa kugahena kuchisoni chao. Kodi inu sindinu m’Kristu otere, mwa mwayi uli onse? Wosakhala m’Kristu sinkhani apa, koma ndi inu monga m’Kristu; kodi muli ndi chidaliro kuti palibe bvuto ndi chipulumutso chanu?Chipulumutso Chingapezeke Pokhapo Ngati Mau a Ubatizo Ndi Mwazi wa Yesu Anenedwa Momveka Bwino


Yesu Kristu wadza kwa ife ndi madzi (ubatizo omwe Ambuye anasenzera machimo onse), mwazi ndi Mzimu, ndipo ali yense olalikira Uthenga Wake Wabwino wa madzi ndi Mzimu ayenera kuchitira umboni zinthu zonse zitatu momveka bwino. Pokha pokha munthu alalikire Mau a chipulumutso a Yesu, amene anadza mwa madzi ndi mwazi, munthu ameneyu sangatsogolere wina wake kuti abadwe mwatsopano. Anthu otero alibe kanthu ndi otsatira chabe a chipembedzo chotchedwa Chikristu. Ndi chifukwa chake ndikutcha Chikristu cha dziko kuti chipembedzo, koma Chikristu cheni cheni ndi chikhulupiliro chomangidwa pa Mau a choonadi, osati chipembedzo chabe.

Kodi Chikristu chingakhale bwanji chipembedzo cha dziko, pamene chipembedzo ndi chopangidwa ndi munthu? Chikristu ndi chikhulupiliro, chomwe ndi choikidwa  m’Mau  a Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo otsirizidwa ndi Mulungu. Ndi kukhulupilira muchikhululukiro cha machimo chomwe Mulungu Mwini wakwaniritsa. Uku ndiye kusiyana pakati pa chikhulupiliro cha Chikristu ndi chipembedzo chabe. Yesu Kristu sanadze pa dziko lino kudzayambitsa chipembedzo, kapena kukhazikitsa Chikristu cha lero cha dziko.

Muyenera kupeza chipulumutso chanu choonadi pokhulupilira mu Uthenga Wabwino wa ubatizo ndi mwazi wa Yesu, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo omwe wapulumutsa ochimwa onse amene akhulupilira mu choonadi cha chipulumutso. Ndipo pamene mwabadwa mwatsopano, muyenera kudzuka ndikuwalitsa nyali ndi Mau a Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo ndikukhala mboni yolimba mtima ya Uthenga Wabwino wa madzi ndi mwazi, kunena kuti, “chipulumutso sichingapezeke pongokhulupilira mu mtanda okha; palibe njira ina ya chipulumutso koma Uthenga wa Mau abwino a chikhululukiro cha machimo!” Kwa onse amene akufunsa inu za chipulumutso choonadi cha chikhululukiro cha machimo, myenera kuwauza iwo kuti ubatizo ndi mwazi wa Yesu ukupanaga Uthenga Wabwino wa choonadi omwe ukulola ali yense kubadwa mwatsopano, ndipo kuti mwazi wa Yesu okha pamtanda si Uthenga weni weni.Ali Yense Amene Akonda Ambuye Mwa Iyeyekha Adzaonongedwa Kumapeto 


Pamene m’Kristu wakhulupilira mwa Ambuye popanda kudziwa Mau a kusinthidwa operekedwa ndi Yesu, ndi kukonda Ambuye mwa iyeyekha, chikhulupiliro chake chili monga chikondi chosakondedwa. 

Lolani ndiunikire izi ndi chitsanzo. Ganizirani kuti mwamira pa madzi pamene m’maoloka Nyanja, ndipo mwatumiza chidziwitso mwachangu ndipo mukufuna kupulumutsidwa. Atafika, opulumutsa wa mundege anaponya chingwe kwa inu kuti akukokeni kuchoka m’madzi, koma m’malo modzimangilira thupi lanu lonse ndi chingwe, munangochigwira ndi manja anu. Izi ndi chimodzi modzi kukonda Yesu mwa inu nokha posakondedwa mobwezeredwa, kunena mwakhungu kuti, “chonde ndipulumutseni ine! Ndikukhulupilira kuti mudzandipulumutsa ine ngati ndangokhulupilira mwa Inu!” Mwa nthawi, anthu otere adzatopa ndi mphamvu zao ndi kusiya chingwe kenako ndi kuonongeka. Izi ziri choncho chifukwa iwo adalila mphamvu zao kukhulupilira mwa Yesu. Musalore nokha kukhala okhulupilira osochera chotere.

Kukonda Yesu mbali imodzi ndi kunena kuti, “Ambuye, ndimakhulupilira mwa Inu! Ndikukhulupilira muchipulumutso cha Yesu Kristu, amene anadza mwazi pamtanda ndi Mzimu!” anthu osawerengeka akonda Yesu mbali imodzi motere. Chifukwa iwo ndi mbuli pa Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo ndipo sadziwa Mau a ubatizo ndi mwazi wa Yesu omwe afufuta machimo onse mu mitima yao, sanagakhulupilire mu chipulumutso cha Ambuye ngakhale pamene ayesera kuchita bwino. Ndipo chifukwa iwo alibe chitsimikizo cha chipulumutso chao, iwo angoitana pa dzina la Ambuye ndi kunena ndi mau ao okha kuti amakhulupilira mwa Iye.

Mwa kusiyana, ife tiri ndi chitsimikizo muchipulumutso chathu chifukwa talandira Uthenga Wabwino oonadi wa madzi ndi Mzimu. Kulankhula chikhulupiliro ndi mau okha ndizosiyana kotheratu ndi kukhulupilira ndi mtima. Akristu onse amene sanabadwe mwatsopano ndipo choncho adakali ndi uchimo mu mitima yao adzaponyedwa kugahena pamapeto pake. Ngakhale iwo akunena kuti adzatsata Ambuye mpaka kumapeto, chifukwa iwo ali ndi uchimo mu mitima yao, adzakanidwa pa tsiku lomaliza. Izi ziri chonchi chifukwa iwo akonda Yesu mbali imodzi. Ndipo chifukwa iwo akhulupilira m’mwazi okha wa Yesu Kristu ndi Mzimu, chikondi chao chosakondedwa kwa Ambuye chidzakhala mwa chabe, adzakanidwa ndi Ambuye ndi kuponyedwa kugahena kumapeto.

Choncho, ngati mukufuna kukhulupilira mwa Yesu molondola, muyenera kumangilira moyo wanu ndi chingwe cha Mau a ubatizo wa Yesu, mwazi Wake, ndi Mzimu, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo; ndipo pamene mwa mangilira moyo wanu muyenera kuzindikira kuti mwamangidwa bwino bwino ndi chingwe cha choonadi. Pamene Mau a chitetezero cha machimo atsika, ali yense wakhulupilira m’Mauwa adzachotseredwa machimo ake onse popanda kulephera.

Kubwerera kuchisanza chopulumutsa chomwe ndangokupatsirani, ganizirani tsopano kuti opulumutsa pandege analankhula kudzera pa chinkuza mau, “mvetserani kwa ine mosamara. Pamene ndagwetsa chingwe ichi, onetsetsani kuti mwadzimangilira thupi lanu lonse molimba, kuti chisamasuke. Kenako chigwireni ndikudikilira. Osakwera pa chingwe mwa inu nokha kupita kundege. Mudzagwa mpaka kufa. Choncho dalilani mau anga, khalani ndi chikhulupiliro ndipo ingodikilirani.” Atamva izi, wina anadzimangilira yekha thupi  lake ndi chingwe monga mwa langizo. Ndipo iye anayembekeza mwa chikhulupiliro. Munthu  ameneyu kenako anapulumutsida ku imfa podalira chingwe chomangiliridwa mozungulira thupi lake.

Motsutsana, tiyeni tinene kuti munthu wina anakana kutsatira langizo, ndi kunena kuti, “musadandaule ndi ine. Simukudziwa mphamvu zomwe ndiri nazo. Simufunika kudandaula chili chonse pa ine. Kuchokera apa ndikoza kukwera ndekha chingwe.” Choncho munthuyu anagwira chingwe ndi kuyamba kukwera mwa iyeyekha. Poyamba, iye anachita bwino, koma pambuyo pake panali bvuto. Ndege inkaulukira pamtunda ndi munthu ogwililira chingwe m’mwamba, ndipo pamapeto pake, iye anatopa moti anataya mphamvu pa chingwecho pamapeto pake. Kodi anthu awiri amenewa ndindani anali ndi chikhulupiliro chabwino?

Anthu awiri onsewa ankayesera kukwera kupita kundege munjira zosiyana. Munthu oyamaba amene anadzimangilira thupi lake ndi chingwe anakwezedwa mpaka kufika kundege ngakhale kuti iye analibe mphamvu pa iyeyekha. Motsutsana, munthu wachiwiri uja amene ankadzikuza ndi mphamvu zake pamapeto pake anatopa ndi kusiya chingwe mpaka kuimfa yake.

Chimodzi modzinso, iwo amene akunena kuti achotseredwa kumachimo ao onse pokhulupilira mwa Yesu Kristu komanso Uthenga Wake Wabwino ndi iwo amene akhulupilira m’Mau a Uthenga Wabwino omwe adza ndi ubatizo ndi mwazi wa Yesu komanso Mzimu, omwe Ambuye kudzera mwa uwo wapulumutsa ochimwa mwangwiro. Kudzera mu Uthenga Wabwino wa madzi ndi mwazi, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo, Ambuye akunena kuti, “ndakupulumutsani mwangwiro chotere ndi madzi, mwazi ndi Mzimu.” Ndipo Iye wabweretsa chipulumutso cha ngwiro kwa onse amene akhulupilira mu Uthenga Wabwino monga m’mene ulili. 

Komabe, iwo amene sakhulupilira mu Uthenga Wabwinowu amanena, kuti, “Ambuye, ndimakhulupilira mwa Inu. Ndingapulumutsidwe ku machimo anga onse kudzera mu mwazi wamtengo wapatali omwe munakhetsa pamtanda. Ngakhale sindikudziwa kali konse ka ubatizo wanu komanso chomwe ukutanthauza, popeza ndakhulupilira m’mwazi wanu ndi Mzimu, izi ndizokwanira. Ndingabadwebe mwatsopano ngakhale kuti sindidziwa chobisika cha ubatizo wanu. Mwazonse, ndi kukhulupilirabe mwa Inu monga Mpulumutsi wanga. Choncho musadandaule kuti ndidzathera mugahena!” Kupatula kukhulupilira mwa Yesu, komabe, anthu otere adakali ndi uchimo m’mitima yao, ndipo choncho adzaponyedwa kugahena mwachidziwikire. Musabvomere nokha kukhala monga iwo. Muyenera kubadwa mwatsopano pokhulupilira m’Mau a chipulumutso, Mau a ubatizo wa Yesu.

Dziunikeni nokha pa Mau oonadi a Mulungu ndi kuona zomwe m’makhulupilira. Ngati mukhulupilira m’mwazi okha wa Yesu ndi Mzimu, ndiye kuti mukufunika Mau a Uthenga Wabwino komanso chikhulupiliro cholola inu kubadwa mwatsopano ndi kupulumutsidwa ku machimo anu onse. Mzimu wa Yesu ndi mwazi Wake sizikwanira kufufuta machimo anu onse. Mau omwe Mulungu Mwini anachitra umboni kuti inu mwabadwa mwatsopano monga m’modzi mwa anthu ake ndi Mau a Uthenga Wabwino a madzi ndi Mzimu. Uthenga Wabwinowu wa chitetezero cha machimo, Mau oonadi a Mulungu a chipulumutso, akunena kuti Yesu anasenza machimo anu onse kudzera mu ubatizo Wake, anapachikidwa ndi kuweruzidwa mpaka kufa chifukwa cha machimo anu m’malo mwanu, ndi kuuka kwa akufa. Ndipo kwa onse amene akhulupilira ndi mtima onse m’Mau a chipulumutso, Mulungu wadalitsa iwo kuti abadwe mwatsopano. Mulungu wapatsa Mzimu Woyera kwa okhulupilira awa, ndi kunena kuti, “ndakahala Mpulumutsi wanu. Ndakupulumutsani inu ndekha. Inu khulupilirani mu ubatizo wanga ndi mwazi, komanso khulupilirani kuti ndine Mulungu. Ndipo choncho mwabadwa mwatsopano. Ndinu ana a Mulungu Atate, ndipo mwachidziwitso, ndakupatsani Mzimu Woyera.”

Komabe, ngati wina sakhulupilira ndi mtima onse mwazonse zitatu zofunika pa chipulumutso-madzi (ubatizo) a Yesu, mwazi Wake (imfa), komanso Mzimu-kenako Mulungu Mzimu Woyera akunena kuti, “simunapulumutsidwe, pakuti simukhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu.” Mtumwi ali yense anachitira umboni kuti chipulumutso cha chitetezero cha machimo chimapezeka kudzera mu ubatizo wa Yesu, mwazi Wake ndi Mzimu.

Kwalembedwa mu 1 Petro 3:21, “Cimenenso cifaniziro cace cikupulumutsani tsopano ndico ubatizo.” Chifaniziro cha chipulumutso ndi Uthenga Wabwino wa madzi, mwazi, ndi Mzimu, onena kuti Yesu anasenza machimo athu onse kudzera mu ubatizo Wake ndipo Iye anaweruzidwa  pamtanda mwa kukhetsa mwazi Wake, ndipo kuti Iye wapulumutsa okhulupilira ake onse ku tchimo lili lonse la dziko kuti akhale Mpulumutsi wathu.

Kulankhula za chipulumutso cha ubatizo wa Yesu, mtumwi Paulo ananena mu Aroma 6:3, “Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwa Kristu Yesu; tinabatizidwa mu imfa yace?” Paulo kenako anapitilira ndi kunena mu ndime ya chisanu, “Pakuti ngati ife tinakhala olumukizidwa ndi Iye m’cifanizidwe ca imfa yace, koteronso tidzakhala m’cifanizidwe ca kuuka Kwake,” ndipo pena pake mu Agalatiya 3:27, iye anati, “Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Kristu mudabvala Kristu.” Motere, atumwi ankakhulupiliranso ndi kulalika Mau a ubatizo wa Yesu, Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo. Kodi chikhulupiliro chanu ndi chopambana kuposa chikhulupiliro cha atumwi? Kodi atumwi anakana ubatizo wa Yesu, omwe Ambuye wathu anasenza machimo onse a dziko? Ai, sichoncho; onse ankakhulupilira mu ubatizo. Inunso muyenera kukhulupilira mu Uthenga Wabwino wa choonadi ndi kupulumutsidwa.Uthenga Wabwino Operekedwa Ndi Mulungu wa Chitetezero Cha Machimo Unakwaniritsidwa Ndi Madzi a Ubatizo wa Ambuye Ndi Mwazi Wake Pamtanda


Yesu anadza pa dziko lino mwa ubatizo Wake ndi mwazi. Ife tonse tiyenra kuwalitsa nyali ya ubatizo ndi mwazi wa Yesu, nyali yoonadi ya chipulumutso, ndipo ife tiyenera kukhulupilira  m’Mau omwe apulumutsa ife-ndiko kunena kuti, mu ubatizo wa Yesu, mwazi Wake pamtanda, komanso umulungu Wake. Tiyenera kuchitira umboni momveka bwino kuti Yesu Mwana wa Mulungu komanso Mpulumutsi wangwiro wa ochimwa onse, ndipo tiyenera choncho kuwalitsa nyali ya Uthenga Wabwino wa ubatizo Wake ndi mwazi. Mulungu watipatsa momveka bwino ife nyali ya chipulumutso, ndipo Iye wauza ife kuti tiwalitse nyaliyi. Tiyenera kulemekeza Lamuloli tsopano.

Ngati wina wake ali ndi tchimo kupatula kuti amakhulupilira mwa Yesu ndi kunena kuti ndi munthu olungama, ndiye kuti munthu otereyu si munthu olungama koma ochimwa. Palibe ochimwa amene angagonjetse dziko. Kutali ndi izo, ochimwa ali yense adzaonongedwa  chifukwa cha uchimo.

Pokha pokha mukhulupilire m’madzi (ubatizo) wa Yesu, machimo anu sangafufutike. Momwemonso, pokha pokha ngati mwakhulupilira m’mwazi wa Yesu, simungamasuke ku chiweruzo cha uchimo kapena kulandira chipulumutso. Yesu Kristu ndi Mulungu Mwini amene anadza pa dziko lino mwa Mzimu Woyera m’mimba mwanamwali Maria, ndipo simungapulumutsidwe pokha pokha mukhulupilire mwa Ambuye ameneyu. Ali yense amene sakhulupilira mwa Yesu ndi mtima wake onse sangakhale olungama mwangwiro ndipo m’malo mwake adzakhala ochimwa. Iwo amene amanena kuti ndi olungama moperewera akuimilira otchedwa kuti “chiphunzitso cha chiyeretso,” kunena kuti Mulungu amaona iwo opanda tchimo ngakhale kuti adakali ndi uchimo. Anthu otere sanabwerebe muchonadi cha Yesu Kristu cha kusinthidwa. Ngakhale Akristu otere akulimbana kuti iwo anabadwa mwatsopano popeza Mulungu amaona iwo opanda tchimo kupatula kuchimwa kwao, iwo ndi mbuli zotheratu pa Baibulo. Anthu otere amaphunzitsa anzao za m’mene angabadwire mwatsopano, koma iwo sangadziphunzitse okha, poti iwo sadziwa!

Ngati mukuganiza kuti Mulungu mwina mwake adzakuonani ngati olungama ngakhale muli ndi uchimo, mukupanga cholakwika cha chikulu. Mulungu wanena kuti okhawo amene ali olungama kotheratu ndiye oongoka, ndipo Iye akuuza ochimwa kuti ndi ochimwa komanso sanabadwe mwatopano. Iye sanena kwa ochimwa kuti ndi olungama chifukwa munthuyu akunena kuti amakhulupilira mwa Iye mwanjira ili yonse. Ngakhale Mulungu ndi wa mphamvu, Iye sanganame. Bvuto ndilakuti Akristu ambiri samvetsetsa komanso alakwitsa Mulungu m’maganizo ao. Okhawo amene Mulungu akunena kuti ndi olungama ndi oyeradi.

Chiphunzitso chopangidwa ndi munthu cha chiyero ndi chopanda ntchito poti ndi choturuka m’maganizo a munthu; si Uthenga Wabwino opangidwa ndi Mulungu wa ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Chiphunzitsochi chimanena kuti Mulungu amaona ochimwa ngati olungama ngakhale Iye adakali ochimwa. Koma Mulungu wathu sanama poitana ochimwa kuti ndi olungama ngakhale iye ali ndi uchimo. Chifukwa nzosatheka kwa Mulungu kunama, Iye saitana ali yense ochimwa kuti ndi munthu olungama, ngakhale kuti munthuyu ndi mu Kristu. Koma kupatula izi, ngati wina wake akuganizabe kuti Mulungu adzamutcha iye munthu olungama chifukwa iye amakhulupilira mwa Yesu muli monse, ndiye kuti iye ndi opusa. Ngakhale anthu sakonda bodza, choncho Mulungunso naye sakonda bodza, Mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi, kodi Iye angaitane munthu kukhala olungama chifukwa chakuti wangokhulupilira mwa Yesu? Ai, sichoncho! Ndikudziwa kuti mukudziwa nokha bwino lomwe kuti Mulungu sangachite zimenezo.

Mwa Mau amene Yesu watipulumutsira ife, kaya ubatizo Wake kapena mwazi Wake watsara, ndiye kuti Uthenga otero ndi opangidwa ndi maganizo a munthu; si choonadi cheni cheni chomwe chapanga ochimwa kukhala olungama. Choncho, pali mtundu umodzi wa anthu omwe chikhulupiliro chao chimalandiridwa ndi Mulungu. Mulungu watsimikiza chikhulupiliro cha iwo amene akhulupilira mu ubatizo wa chipulumutso omwe Yesu analandira pa dziko lino, iwo amene akhulupilira ndi mtima onse mu Uthenga Wabwino wa chitetezero cha machimo. Chikhulupiliro choti Yesu Kristu anadza pa dziko lino ndi kulandira machimo onse a ali yense mwakubatizidwa; chikhulupiliro choti Iye anaweruzidwa pamtanda mwa kukhetsa mwazi Wake atasenza machimo onse a dziko; komanso chikhulupiliro choti Iye  anauka kwa akufa-ndi iwo amene ali ndi chikhulupiliro chotere m’Mau amenewa a chitetezero cha machimo omwe Mulungu awapulumutsa monga anthu Ake olungama.

Kukanakhala kuti Yesu anafa pamtanda popanda ngakhale kusenza machimo athu kudzera mu ubatizo Wake pa dziko lino, ndikungonena kuti, “ndidzakuferani inu; ingokhulupilirani mwa Ine,” ndiye kuti Iye sakanakhala Ambuye chabe, ndipo Ambuye akanaonedwa ndi ife monga olephera komanso Mulungu osintha sintha. Chifukwa chakuti ngati Ambuye akananena kuti Iye wafufuta machimo onse a dziko popanda kuwalandira machimowo kudzera mu ubatizo Wake, ndiye kuti chipulumutso Chake chikanakhala chosokonezeka kwa ife kuti tikhulupilire.

Ambuye anati, “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu” (Mateyu 11:28). Yesu angaitane ochimwa onse kumpulo Wake chifukwa Iye wapulumutsa iwo ku machimo ao onse kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi. Mulungu saona ali Yense amene wakhulupilira m’mwazi okha wa pamtanda.

Ufumu wa Mulungu uli ndi choonadi, chilungamo, chikondi komanso kuleza mtima, ndipo mulibiletu bodza lili lonse. Kusiyana ndi dziko lino lapansi, palibe tchimo lingapezeke mu Ufumu wakumwamba. Kwalembedwa, “Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mau m’dzina Lanu, ndi m’dzina Lanunso kuturutsa mizimu yoipa, ndi kucita m’dzina Lanunso zamphamvu zambiri?” (Mateyu 7:22). Koma Mulungu sanazindikire machitidwe olungama a munthu ali yense monga chipulumutso chake.

Mulungu siofewa mtima monga tikuganizira (Mateyu 7:23). Pamene tsiku la chiweruzo lafika, anthu ambiri adzanena kuti, “Ambuye, ndinapereka kwa inu nyumba ziwiri ndipo ndinakhuthula moyo wanga kwa Inu. Kodi simukundiona tsopano? Kodi simunkandiona ine kupereka moyo wanga ngati nsembe kuti ndisakukaneni Inu?”

Koma Ambuye adzanena kwa iwo, “chokani kwa Inu! Ochimwa ngati inu simungabwere kuno!”

“Koma ndinaphedwa chifukwa cha Inu!” 

“kuphedwa kotani? Unafa chifukwa chofuna kuonetsa kuuma mtima kwako. Kodi ndinachitira umboni kuti ndiwe m’modzi wa anthu anga? Ndinapulumutsa ochimwa kudzera m’Mau a Uthenga Wabwino wa Ubatizo wanga, mwazi wanga, ndi Mzimu. Kodi Mau a Uthenga Wabwinowu anachitira umboni kuti ndiwe m’modzi wa anthu anga? Kodi unadziwa za Mau amenewa? Kodi unaphunzirapo za iwo? Kodi m’malo mwake sunaime molimbana ndi Mauwa? Choncho ndingachite chiani tsopano, popeza unakhulupilira mwa iwe wekha kuti unapulumutsidwa ngakhale Mau anga sanachitire umboni pa izi? Sunaphedwe kuteteza chikhulupiliro chako mu Uthenga Wabwino wa madzi a ubatizo wanga, mwazi wanga ndi Mzimu; kutali ndi izo imfa yako ili mwa chabe. Unandikonda Ine mwa iwe wekha, kukhulupulira m’mwazi wanga pamtanda ndi Mzimu mwa chabe. Kodi ukuzindikira tsopano zomwe wachita? Choncho udzaponyedwa kugahena!” Izi ndi zomwe Ambuye adzanena kwa onse amene akhulupilira mwa iwo okha kuti ndi olungama ngakhale ali ndi tchimo.

Kwa ife obadwa mwatsopano, kuti chipulumutso chathu ndi chobvomerezeka ndi Mulungu zikunenedwa m’Mau Ake. Zoona zakuti ndife anthu olungama zikunenedwa m’Mau olembedwa a Mulungu a madzi ndi Mzimu.

Kwalembedwa, “Iye amene amkulupilira Mwana wa Mulungu ali nao umboni mwa iye; iye osakhulupirira Mulungu anamuyesa Iye wonama; cifukwa sanakhulupirira umboni wa Mulungu anaucita wa Mwana Wace” (1 Yohane 5:10). Mulungu ananena apa kuti iwo amene akhulupilira mwa Mwana Wake ali ndi umboni mwa iwo. Inenso, ndili ndi umboni mwa ine. Ndipo Mau a umboni akunena motere: “chifukwa cha ife, Mulungu Mwini anadza pa dziko lino monga Mpulumutsi mu thupi la munthu kudzera mu thupi la namwali Maria ndipo Iye anadza mwa Mzimu Woyera; pa dzaka makumi atatu, Iye anasenza machimo onse a dziko mwa kubatizidwa ndi Yohane Mbatizi mwa njira ya kuika manja monga Chipangano Chakale; Iye atasenza machimo a dziko, Iye anaweruzidwa pamatanda m’malo mwa ochimwa; ndipo Iye anauka kwa akufa m’masiku atatu kutipatsa ife moyo.” Mwanjira imeneyi, Ambuye wapulumutsa okhulupilira Ake ku uchimo.

Kukanakhala kuti Ambuye sanauke kwa akufa ndipo m’malo mwake ndiokwiriridwabe m’manda, kodi Kristu wakufa akanachitira bwanji umboni? Koma Ambuye anauka! Choncho Yesu wakhala Mpulumutsi wa okhulupilira Ake onse, ndipo Ife tapulumutsidwa ndi kukhala anthu olungama amene mitima yao ndiyopanda tchimo kotheratu. Mitima yathu yayera monga matalala.

Chifukwa Yesu wapulumutsa ife mu njira yonenedwa m’Chipangano Chakale, tapeza chipulumutso chathu pokhulupilira moyenera kudzera mu Uthenga Wabwino wa ubatizo wa Yesu komanso mwazi Wake omwe Iye wachitira umboni momveka bwino m’Chipangano Chatsopano. Ndiri ndi umboni mkati mwa ine, muli ndi umboni mkati mwanu, ndipo ali yense amene wapulumutsidwa ali ndi umboni mkati mwake. Oyera mtima obadwa mwatsopano amakhulupilira mu ubatizo wa Yesu mosanjenjema ndipo sanyalanyaza ubatizo. Mwapulumutsidwa ngati mwakhulupilira mu chili chonse chomwe Yesu anachita kwa inu, osasiya chili chonse.Chikhulupiliro Cha Iwo Amene Ayesa Mulungu Kukhala Wonama


 Kwalembedwa, “Iye wosakhulupirira Mulungu anamuyesa Iye wonama.” Mtumwi Yohane akunena momveka bwino kuti iwo amene sanakhulupilire zonse zomwe Mulungu wachita kwa iwo-ndiye kuti, iwo amene akukhulupilira mwa Yesu posiya madzi Ake-akupayesa Mulungu kukhala wabodza kumapeto. Pamene anthu otere auzidwa kuti Yesu anachotsa machimo onse a dziko, iwo amanena kuti, “izi sizoona. Ambuye anachotsa tchimo lachibadwa lokha, ndipo choncho tiyenera kupemphera mapemphero akulapa ku machimo athu amasiku onse; Ambuye adzafufuta machimo athu akutsogolo nthawi zonse pamene taulula machimowo.” Anthu otere akukana ubatizo wa Yesu, ndipo popeza okhulupilira chotere akuyesa Mulungu kukhala wonama, onse adzaweruzidwa kamba ka tchimoli.

Munthu saponyedwa kugahena chifukwa chochita machimo ambiri, koma iye amakanidwa chifukwa sanakhulupilire mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, ndipo motero kuyesa Mulungu kukhala wonama. Anthu otere amene sakhulupilira mu ubatizowu wa Yesu ali ndi tchimo mu mitima yao, ndi chifukwa chake amanena kuti, “kodi ndinganene bwanji kuti ndilibe tchimo pamene ndimapitiliza chabe kuchimwa?” Mwanjira imeneyi iwo akupanga Mulungu kukhala wonama mpaka kumapeto, kungofuna kulangidwa kamba ka tchimoli. 

Ndinafunsapo mkulu wampingo wina kuti, “kodi machimo anga angachoke ngati ndakhulupilira mwa Yesu?”

“Inde, nzotheka,” anatero mkulu wampingo.

“Ndiye kuti uyenera kukhala opulumutsidwa, popeza Baibulo imanena kuti Yesu anachotsa machimo onse a dziko, ndipo Iye anatsiriza ntchito yonse ya chipulumutso?” 

Mkulu wampingo anayankha, “Inde, ndichoncho!”

Ndinamufunsa kachiwiri, “Ndiye kuti muyenera kukhala opanda tchimo sichoncho?”

“Inde, ndilibe tchimo tsopano ndikuyamika mwazi wa Yesu.”

“Nanga chidzachitika ndi chiani mukachimwa mtsogolo?”

Iye anayankha, “Ndidzakhala ochimwa. Nanga munthu angakhale bwanji opanda tchimo? Popeza tonse ndife anthu, nzosatheka kuti ife tisachite tchimo. Koma tiyenera kulapa nthawi zonse pamene tachita tchimo lili lonse, ndipo kenako uchimowo udzachoka.”

“Nanga apa tsopano? Kodi muli ndi tchimo lili lonse?”

“Inde ndili ndi tchimo.”

“Ndinu oyera mtima nanga?”

“Ai, ndine ochimwa.”

“Nanga ndindani amene adzapita kumwamba, munthu olungama kapena ochimwa?”

“Ndi olungama amene adzapita kumwamba.”

Choncho ndinamufunsa iye komaliza, “nanga iwe udzapita kuti tsopano?” atasowa mau, mkulu wampingo sanayankhenso funso lili lonse ndipo anandisiya ine ndikudandaula mwachisoni kwa iye. Ndi chikhulupiliro cha anthu otere chomawe chapanaga Mulungu kukhala wonama, ndipo choncho iwo adzaponyedwa kugahena poyesa Mulungu kukhala wonama.Ali Yense Wokhulupilira mu Uthenga Wabwino Wakale Sakana Umulungu wa Yesu


Monga Baibulo likunena, “Iye amene amkulupilira Mwana wa Mulungu ali nao umboni mwa iye; iye osakhulupirira Mulungu anamuyesa Iye wonama; cifukwa sanakhulupirira umboni wa Mulungu anaucita wa Mwana Wace” (1 Yohane 5:10), tonse tili ndi umboni omveka bwino pa chipulumutso chathu. Ali yense amene wapulumutsidwa kudzera mwa madzi ndi Mzimu amakhulupilira mu choonadi choti Yesu anabadwa pa dziko lino kudzera mwa thupi la namwali Maria mwa Mzimu Woyera, kuti machimo ake onse anaperekedwa pa Yesu pamene Iye anabatizidwa, ndipo kuti Yesu anafufuta machimo onse mwakufa pamtanda ku machimo a dziko. Anthu otere amakhulupilira kuti chipulumutso chimapezeka mwa kukhulupilira mwa Yesu amene anadza mwa madzi, mwazi, ndi Mzimu. Okhawo amene akhupilira Yesu Kristu amene anadza mwa Mzimu, madzi, ndi mwazi angapeze umboni onena pa chipulumutso chake pamaso pa Mulungu.

Baibulo likunena kuti, “Kuti Uthenga Wabwino wathu sunadza kwa inu m’mau mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m’kucuruka kwakukuru” (1 Atesalonika 1:5). Satana amakonda kuona anthu akulalikira mwazi wa Yesu Kristu okha, ndipo iye akunyenga anthu ambiri kuti akhulupilire m’mwazi okha wa Yesu. Muyenera kuzindikira apa kuti nthawi ino ndi nyengo ino, mdierekezi akugwira ntchito m’mipingo yapamwamba ya dziko lapansi m’malo mwamasautso kuti anyenge anthu kukhulupilira mu Uthenga omwe ulibe Ubatizo wa Yesu, omwe ndi chifaniziro cha chipulumutso (1 Petro 3:21).

Uthenga Wabwino omwe satana amaopa kwambiri mu dziko lino ndi Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu. Mdierekezi amathawa pamene wakumana ndi ali yense amene ali ndi chikhulupiliro m’Mau a ubatizo wa Yesu, mwazi Wake pamtanda, komanso umulungu Wake monga Mwana wa Mulungu.

Pamene mwaonera kanema ya The Exorcist, mungathe kuona a nsembe a Chikatolika akuchita mwambo othamangitsa mizimu yoipa, kupemphera kwambiri ndi kugwedeza mtanda kwa mizimu yoipa, koma ngakhale ansembewa sakusiyana ndi mizimu yoipa ndipo onse akufa. Mutsutsana, nzosatheka kwa ali yense amene wabadwadi mwatsopano, komanso amene chipulumutso chake chachitiridwa umboni ndi Mulungu Mwini, kugonjetsedwa ndi satana. Obadwa mwatsopano amakhala pansi mwachete, ndi kuika chikhulupiliro chao m’Mau olembedwa, iwo amalamula mizimu yoipa kuti ichoke mwabata. Ngati mdierekezi akuyesera kunyenga inu, ingoyankhulani Uthenga Wabwino wakale wa madzi ndi Mzimu mwabata, kunena kwa satana kuti, “kodi ukuzindikira kuti Yesu anachotsa machimo anga onse?” mdierekezi kenako sadzakhala ndi mtendere ndipo adzathawa.

Kodi umboni onena za Mwana wa Mulungu ndi chiani? Kodi si Uthenga Wabwino wa chipulumutso onena kuti Yesi Kristu anadza pa dziko lino mwa Mzimu Woyera, kusenza machimo athu onse pa thupi Lake kudzera mu ubatizo Wake, ndi kukhetsa mwazi Wake mpaka kufa pamtanda m’malo mwathu? Munthu amanama kwa Mulungu chifukwa iye sanakhulupilire m’Mau amenewa a umboni onenedwa ndi Mzimu, madzi, ndi mwazi; ndipo ali yense okhulupilira ndi kulalikira uthenga wabodza amasandulika yekha kukhala m’neneri onyenga.

Baibulo likunena mu 1 Yohane 5:11, “Ndipo uwu ndi umboniwo, kuti Mulungu anatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene uli mwa Mwana Wace.” Monga Mulungu watipatsa ife moyo wosatha ndipo moyowu uli mwa Mwana Wake, ali yense amene walandira moyo wasathawo ndi munthu olungama, ndipo iye adzakhala kwamuyaya. Ngati mwakhulupilira mu Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu, ndiye kuti mwalandiranso moyo wosatha.

Mtumwi Yohane, Paulo komanso Petro ankasiyanitsa anthu amene abadwa mwatsopano kwa iwo amene sanabadwe mwatsopano. Nanga kodi, atumiki alero a Mulungu angazindkire bwanji anthu obadwa mwatsopano? Kodi mungasiyanitse bwanji atumiki eni eni a Mulungu komanso anthu Ake? Iwo amene alandira chipulumutso komanso moyo wosatha kudzera mwa madzi ndi Mzimu angasiyanitse opulumuka ndi osapulumuka. Chifukwa chakuti iwo ali ndi Mzimu Woyera komanso Mau olembedwa a Mulungu mwa iwo.

Ngati wina wake ali mu ofesi ya mpingo, monga mbusa kapena mkulu wampingo, sanagasiyanitse kaya membala wa mu mpingo wake ndi oyera mtima kapena ai, ndiye kuti munthu ameneyu sanabadwe mwatsopano, ndipo iye ndi munthu opanda moyo amene alibe Mau a madzi, mwazi ndi Mzimu mwa iye. Iwo amene alibe moyo mwa iwo sangasiyanitse motere, ndipo monga munthu wakhungu, iwo amangophunthwa popanda kudziwa choyenera ndi cholakwika. Motsutsana, wina wake amene wapulumutsidwadi angasiyanitse munthu oyera mtima kapena ai. 

Izi ndi zofanana ndi kuyesa kusiyanitsa mitundu yosiyana mu mdima wa ndiweyani. Munthu wa khungu sanganene kuti chobiliwira ndi chobiliwira kapena choyera ndi choyera chifukwa maso ake saona, ndipo chifukwa chake iye sangaone, sanganene kusiyana pakati pa mitundu iwiriyi. Mwakutsutsana, wina amene ali ndi diso lakuthwa angasiyanitse pomwepo. Iye akudziwa kuti pali kusiyana koonekeratu pakati pa chobiliwira ndi choyera chifukwa iye waona.

Pokha pokha ife obadwa mwatsopano tawalitsa nyali ndi kuchitira umboni za ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, Uthenga Wabwino wa chikhululukiro cha machimo, anthu osawerengeka azaonongeka. Ngati tingalore izi kuchitika, ndiye kuti kutali ndikukondwera nafe, Mulungu adzadzudzula ife pokhala akapolo a mwano. Tiyenera kuwalitsa nyali momveka bwino ndi mwa nzeru. Ndi makonda kubwereza mfundo imeneyi chifukwa anthu ambiri samamvetsetsa mpaka itafotokozedwa kwa iwo mwatsatanetsatane kawiri kawiri. Mwachisanzo simungamuyambitse munthu osaphunzira kotheratu ndikuyembekeza iye kuyamba kulemba pomwepo musanamphunzitse iye ngakhale afabeti. Pamene chilankhulo chikuphunzitsidwa, munthu ayenra kuyamba ndi chikhazikitso chofotokoza kuti afabeti ndi chiani, komanso m’mene malembo ndi ndime zimamangidwira mwakuphatikiza mau kuti alumikizane. Chimodzi modzi, Baibulo liyenera kuphunzitsidwa momveka bwino kuyambira pachiyambi.

Motere, ubatizo wa Yesu uyeneranso kufotokozedwa momveka bwino komanso mobwereza. Zomwe ndalemba mu bukuli si za m’mutu mwanga, koma zalalikidwa kuchokera pa Mau, otsimikizidwa ndi malembo eni eni, komanso zamangidwa pa chikhazikitso cha m’Baibulo.

Chipulumutso kwa ochimwa chakwaniritsidwa kotheratu. Chifukwa machimo onse a dziko anaperekedwa pa Yesu pamene Iye anabatizidwa, Iye anakwiriridwa m’malo mwa ochimwa; chifukwa machimo onse a dziko anaperekedwa pa Yesu, kuti onse a ife amene takhulupilira mu izi tatsukidwa ku machimo a m’mitima yathu; ndipo choncho, ndi chokhulupiliro mu Uthenga Wabwino oyamba omwe walola ali yense kusamalilidwa m’manja mwa Mulungu. Uthenga Wabwino wakale uwu okwaniritsidwa ndi Ambuye ukulola ali yense kubadwa mwatsopano mwa madzi, mwazi, ndi Mzimu, ndipo ndiri ndi chiyembekezo komanso kupemphera kuti nonse mukhulupilire mu Uthenga Wabwinowu ndi kulowa mkati.