Chichewa 1
Rev. Paul C. Jong
Obwohl die Covid-19-Pandemie beendet ist, gibt es immer noch Schwierigkeiten beim Versenden oder Empfangen unserer gedruckten Bücher per Post aufgrund verschiedener internationaler Situationen. Wenn sich die internationale Situation verbessert und sich der Versand normalisiert, werden wir den Versand gedruckter Bücher wieder aufnehmen.
OH INDE! NDINALI OCHIMWA KOMA TSOPANO NDINE MWANA WA MULUNGU OPANDA UCHIMO POKHULUPILIRA MU UTHENGA WABWINO WA MADZI, MWAZI NDI MZIMU
Ndikuthokoza Mulungu posindikiza buku lapadera lotchedwa KODI MWABADWADI MWATSOPANO MWA MADZI NDI MZIMU? Kudzera mwa mtumiki Wake REV PAUL C.JONG.
Kudzera mu kuwerenga buku limeneli, KODI MWABADWADI MWATSOPANO MWA MADZI NDI MZIMU? la REV PAUL C. JONG, ndamvetsetsa motheratu kuti ndinedi ndani monga munthu kupatula Yesu Kristu. Kuti ndinabadwa wa uchimo kwambiri, ndipo ndinaikidwira ku gahena zonse chifukwa cha machimo anga. Koma mathokozo akhale kwa Mwana Obadwa Yekha wa Mulungu, Yesu Kristu amene anadza ku dziko lino lapansi kusandulika m’thupi la munthu, ndipo pa zaka za 30 kupita ku Mtsinje wa Yordano kukakumana ndi Yohane Mbatizi amene anaimilira monga woimirira wa mtundu wa anthu komanso mkulu wa nsembe wotsiriza pa dziko lapansi pamene Iye anabatiza Yesu Kristu kuti apereke machimo anga onse otengera, akale, atsopano ndi a mtsogolo pa thupi la Yesu Kristu kudzera mu njira ya kuika kwa manja monga yodzodzedwa ndi Mulungu Atate M`chipangano Chakale mu (Levitiko 1:1-4, 16 ndime ya 21) yomwe imafanana ndi ubatizo wa Yesu kudzera mwa Yohane Mbatizi mu (Mateyu 3:13-17). Chifukwa chakuti tsopano ndimakhulupilira mu Choonadi chimenechi kuti Yesu Kristu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi kuti atenge machimo anga onse komanso machimo a aliyense padziko lapansi ndi kupita pa mtanda kuti alipire mphotho ya machimo anga, ndipo pa tsiku lachitatu kuukitsidwa kuti apereke moyo watsopano, ndakhala tsopano mwana wa Mulungu wopanda uchimo komanso olungama. Aleluya!! Ulemelero wonse ndi Ulemu ziperekedwe kwa Yesu Kristu.
Ndikupereka mathokozo anga kwa Mtumiki woona wa Mulungu, Rev. Paul C. Jong, pondidalitsa ine komanso dziko lonse lapansi ndi buku lapadera limeneli lokhala ndi mau enieni a chipulumutso omwe tsopano andipatsa ine mwayi wolowa Kumwamba monga ulendo wanga. Amen.
Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Kristu akupatseni inu chisomo ndi mtendere ngakhale pamene inu mwadza kudzaphunzira ndi kukhulupilira mu choonadi cha uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, Ame!
Ndikupereka mathokozo anga kwa Mulungu chifukwa cha buku lililonse lauzimu lolembedwa ndi Rev. Paul C. Jong. Pakuti kudzera m’mabuku Ake, Mulungu wafotokoza chipulumutso chathu ku uchimo mu njira yophweka. Ulemelero ukhale kwa Mulungu.
Lero anthu ambiri sadziwa Chipulumutso choona chimene Yesu Kristu wabweretsera mtundu wa anthu, ndipo izi zili choncho chifukwa chakuti anthu ambiri amakonda kubisa umunthu wao weniweni, ndipo m’malo mwake iwo amayesetsa mwakhama kufika kwa Mulungu ndi zokumva zao zathupi kuganizira za mtanda wa Yesu wokha, kuganiza kuti, O Ambuye wanga Yesu munandifera ine, pepani, chonde ndikhululukireni, sindidzachimwanso, inde Ambuye ndikulonjeza kuti sindidzachimwanso. Zimene ndi zoipa kwambiri! Pamene anthu amenewo kwenikweni akudziletsa okha kukumana ndi Mulungu woona amene anadza ndi Uthenga Wabwino wa choonadi wa Madzi, Mwazi ndi Mzimu. Choncho, ndikukudandaulirani inu kuti mudziwe kuti kulira kwambiri chifukwa cha kukhetsa mwazi kwa Yesu, kutengeka mtima ndi nyimbo za uthenga wabwino zosakwanira ndi kupereka tsiku lililonse mapemphero akulapa komanso kuyesa kuchita ntchito zabwino, sizingakutsogolereni inu kuti mukumane ndi Mulungu m’modzi yekha woona amene anadza ndi Uthenga Wabwino wa choonadi wa madzi ndi Mzimu(Yohane 3:5).
Koma, mwamwayi wokwanira inu mudakali ndi mwayi wobwerera kuchokera ku kudzinyenga nokha ngati inu mungadzichepetse chabe nokha podziwa moona mtima khalidwe lanu lenileni la uchimo(Marko 7: 21-23) ndi kuvomera kuti ndinu ndani mapaso panu ndi pamaso pa Mulungu. Motero pochita choncho, ndi mitima yodzichepetsa, kenako Mulungu woona adzakupatsani inu Uthenga Wabwino wa choonadi wa madzi ndi Mzimu umene uli ndi ubatizo wa Yesu wochokera kwa Yohane (kumene Iye anatsuka machimo a dziko lapansi), imfa Yake pa Mtanda (pamene Iye analipira mphotho yonse ya uchimo) ndi Mzimu (amene Iye anaukira kuti apereke Moyo Watsopano kwa aliyense amene amakhulupilira). Kuyambira pamenepo, pokhulupilira mu Uthenga Wabwino woona umenewu wa madzi ndi Mzimu, machimo a mu mtima mwanu adzasowa motheratu ndipo inu kenako mudzapeza mwayi wokhala mwana wa Mulungu mulimonse, kuyamba kuyandikira kwa Iye ndi mtima woyera. Aleluya!
Wogwira Nao Ntchito, Zambia