Search

Κριτική Βιβλίων

KUPULUMUTSIDWA NDI MAU OLEMBEDWA A MADZI NDI MZIMU A YESU

  • Brenda Tembo
  • Zambia
  • 1703
  • 02/16/2024

English 63

Sermons on Hebrews (II) - DO YOU KNOW THE INTENTION OF THE AUTHOR OF THE BOOK OF HEBREWS?

Rev. Paul C. Jong

  • ISBN9788928200399
  • Σελίδες383
  • Βαθμολογία

KUPULUMUTSIDWA NDI MAU OLEMBEDWA A MADZI NDI MZIMU A YESU
Ndine omangiriridwa mu Mzimu wanga kudzera mu chikhulupiriro changa mu uthenga wabwino wa Choonadi wa madzi ndi Mzimu powerenga buku la Rev. Paul C Jong lotchedwa kuti, KODI MUKUDZIWA CHOLINGA CHA MLEMBI WA BUKU LA AHEBRI?
Kudzera mu kuwerenga buku limeneli, ndamvetsetsa kuti Mulungu sadzasinthadi konse, ndipo Iye amalankhula kwa ife kudzera kokha m’Mau Ake olembedwa a Choonadi. Akunena mu Ahebri Mutu 1, kuti Mau a Mulungu a chipulumutso anachitiridwa umboni kwa aneneri komanso kwa makolo athu m`manenedwe ambiri ndi mosiyana-siyana kale. Si ena kuposa Mau enieni oona amenewa a chipulumutso omwe amachitira momveka bwino kuti Yesu Kristu ndi Mpulumutsi wa mtundu wa anthu, amene anadza monga Mwanawankhosa wamuyaya wa nsembe amene ananeneredweratu monga nyama yopanda chirema yoperekedwa ndi Mkulu Wansembe Aroni ndi mbadwa zake amene anaima monga oimilira a anthu a Israyeli kuti asamutsire machimo ao onse pa thupi Lake poika manja pa mutu wake monga njira yodzodzedwa ya Umulungu. Kenako nyama inkaphedwa kuti itetezere kapena kulandira chiweruzo m`malo mwa Aisrayeli pophedwa mpaka kufa kapena inkatumidwa m’chipululu, kumene iyo inkayendayenda mozungulira mpaka kufikira imfa yake, motero kupatsa Aisrayeli chikhululukiro cha Uchimo ndi mwazi wake wa pachaka (Levitiko 16:29). Motero chimenechi chinali chithunzithunzi cholozera chenicheni chakudza ngakhale Yesu Kristu. Motero, mofanana, Yesu Kristu wapereka chikhululukiro chonse cha machimo kwa mtundu wonse wa anthu polandira ubatizo Wake kuchokera kwa Yohane Mbatizi Mkulu Wansembe wotsiriza padziko lapansi, amene anapereka machimo adziko lapansi ndi njira yomweyo ya kuika kwa manja ake pa mutu wa Yesu Kristu pa ubatizo Wake, kenako Yesu anavomera machimo onse adziko lapansi pa ubatizo Wake monga Mwanawankhosa wamuyaya wa nsembe, kenako, potero anapachikidwa pa Mtanda kuti alipire mphotho ya machimo athu pokhetsa mwazi Wake wamtengo wapatali, kenako Iye anauka pa tsiku lachitatu kuti apereke moyo wonse watsopano kwa aliyense amene amakhulupilira m’Mau olembedwa oona amenewa a Mulungu ochitidwa umboni monse kale kwa makolo athu m`manenedwe ambiri ndi mosiyana-siyana komanso Mchipangano Chatsopano monga pangano lolonjezedwa lokwaniritsidwa ndi Mulungu (Macitidwe A Atumwi 3:24-26) Aleluya!
Brenda Tembo, Zambia.