• All e-books and audiobooks on The New Life Mission website are free
  • Explore multilingual sermons in global languages
  • Two new revised editions in English have been released
  • Check out our website translated into 27 languages
Search

Sermons

Mutu 1: Uchimo

[1-1] Choyamba Ife Tiyenera Kudziwa Machimo Athu kuti Tiomboledwe (Marko 7:8-9, 20-23)

2021.04.27 259
Choyamba Ife Tiyenera Kudziwa Machimo Athu kuti Tiomboledwe (Marko 7:8-9, 20-23)
(Marko 7:8-9)
“Musiya lamulo la Mulungu(God), nimusunga mwambo wa anthu. Ndipo ananena nao, Bwino mukaniza lamulo la Mulungu(God), kuti musunge mwambo wanu.”
 
(Marko 7:20-23)
“Ndipo anati, Chotuluka mwa munthu ndicho chidetsa munthu. Pakuti m’kati mwake mwa mitima ya anthu, mutuluka maganizo oipa, zachiwerewere, zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa: zoipa izi zonse zituluka m’kati, nkudetsa munthu.”
 
 
Choyamba, ndikufuna nditanthauzire kuti uchimo ndi chiyani. Pali machimo otanthauzidwa ndi God, komanso pali machimo otanthauzidwa ndi anthu. Mau akuti uchimo, mu Chigiriki, amatanthauza ‘Kuphonya cholinga’. Imatanthauza kusapanga izo molondola. Ndi uchimo ngati ife sititsata malamulo a God molondola. Tiyeni choyamba tione pa machimo otanthauzidwa ndi mtundu wa anthu.
 
Kodi uchimo ndi chiyani?
Ndi kuswa malamulo a God.
 
Ife timayeza uchimo malingana ndi chikumbu mtima chathu. Mwanjira ina, si kulakwira lamulo la God koma timaweruza molingana ndi mbiri ya munthu, mtima wake, ndi chikumbumtima chake.
Uwo umaweruzidwa ndi aliyense payekha. Choncho, m’chitidwe omweo ungatengedwe kapena sungatengedwe kukhala uchimo kutengera ndi miyezo yake ya munthu. Ichi ndi chifukwa chake God watipatsa ife ndime 613 za Lamulo kuti zizigwiritsidwa ntchito monga muyezo oweruzira.
Chithunzi chili pansichi chikusonyeza machimo a mtundu wa anthu. 
 
Lamulo la dziko, lamulo la munthu
Chikumbumtima cha munthu 
Lamulo la God 
 Makhalidwe Abwino, chikhalidwe cha anthu
 
Choncho, ife sitiyenera kuika miyezo pa zikumbumtima chathu. 
Machimo a zachikumbumtima zathu sagwirizana ndi zimene God wazifotokoza kukhala uchimo. Choncho, ife sitiyenera kumvera zikumbumtima zathu koma m’malo mwake kuika miyezo ya uchimo pa malamulo a God.
Aliyense wa ife ali ndi lingaliro lake kuti uchimo ndi chiyani. Ena amatenga uwo kukhala zolakwa zawo, ndipo ena amatenga uwo kukhala maganizo okhota.
Mwachitsanzo, ku Korea, zimatengedwa ngati udindo wa ana kuphimba manda a makolo awo ndi udzu, kudula udzu ndi kusamalira manda bwino mpaka iwo eni atamwalira. Koma ku malo a mtundu wachikale ku Papua New Guinea, iwo amalemekeza makolo awo akufa pogawana thupi ndi ziwalo zabanja ndi kudya ilo. (Sindikudziwa ngati iwo amaphika ilo kapena ai asanadye ilo.) Zikuoneka kuti amaletsa thupi kudyedwa ndi mphutsi. Miyambo imeneyi imasonyeza kuti lingaliro la umunthu la uchimo lingasiyane kwambiri.
Choncho ndi chimodzimodzinso ndi zonse chomwe ndi Chabwino komanso kuti uchimo ndi chiyani. Komabe, Baibulo limatiuza kuti ndi uchimo kusamvera malamulo Wake. “Musiya lamulo la Mulungu(God), nimusunga mwambo wa anthu. Ndipo ananena nao, Bwino mukaniza lamulo la Mulungu(God), kuti musunge mwambo wanu.” (Marko 7:8-9) God sasamala momwe ife timaonekera kunja. Iye amayang’ana mkati mwa mitima yathu.
 
 
Miyeso anuokha ndi Uchimo pamaso pa God
 
Kodi tchimo lalikulu kwambiri ndi chiyani?
Ndi kunyalanyaza Mau a God.
 
Ndiloleni ndikuuzeni kuti uchimo ndi chiyani pamaso pa God. Ndi kulephera kukhala moyo malinga ndi chifuniro cha Wake. Ndi kusakhulupirira Mawu a Wake. God anati ndi tchimo kukhala moyo ngati Afarisi, amene anakana malamulo a God ndi kuyika chifunika chachikulu pa ziphunzitso za miyambo. Ndipo Yesu anatenga Afarisi kukhala achiphamaso.
“Kodi ndi God uti amene inu mumakhulupilira? Kodi inu mumandilemekezadi ndi kundipatsa ulemu Ine? Inu mumadzitamandira ndi dzina langa, koma kodi inu mumandilemekezadi Ine?” Anthu amayang’ana kokha maonekedwe akunja ndi kunyalanyaza Mau Wake. Ndipo ndi uchimo pamaso Wake. Tchimo lalikulu kwambiri ndi kunyalanyaza Mau Wake. Kodi inu mukudziwa zimenezi? Ilo ndiye tchimo lalikulu kwambiri la machimo onse.
Zofooka zathu ndi zolakwa zokha, mphulupulu chabe. Zolakwa zomwe ife timapanga komanso zolakwa zomwe ife timachita chifukwa cha kupanda ungwiro kwathu si machimo aakulu, koma zolakwa. God amasiyanitsa machimo ndi zolakwa. Iwo amene amanyalanyaza Mau Wake ndi ochimwa ngakhale iwo ali opanda zolakwa. Iwo ndi ochimwa aakulu pamaso pa God. Icho ndi chifukwa chake Yesu anadzudzula Afarisi.
Mu Mabuku a Chilamulo kuchokera mu Genesis mpaka Deuteronomo, muli malamulo amene amatiuza ife zochita kapena zosachita. Iwo ndi mau a God, malamulo Wake. Ife sitingawasunge iwo 100%, koma ife tiyenera kuwazindikira iwo monga malamulo Wake. God wapereka iwo kwa ife kuchokera kuchiyambi, ndipo ife tiyenera kuvomera iwo motero.
“PACHIYAMBI panali Mau, ndipo Mau anali kwa Mulungu(God), ndipo Mau ndiye Mulungu(God).” (Yohane 1:1) Kenako Iye anati, “Ndipo anati Mulungu(God), Kuyere; ndipo kunayera.” (Genesis 1:3) Iye analenga chilichonse. Ndipo Iye anakhazikitsa Lamulo. 
“Ndipo Mau anasandulika thupi nakhazikika pakati pa ife, ndipo Mau ndiye Mulungu(God).” (Yohane 1:1, 14) Kodi, ndiye, God amadzionetsa Yekha bwanji kwa ife? Iye amadzionetsa Yekha kwa ife kudzera m’malamulo Wake. God ndiye Mau, ndipo Iye amadzionetsa Yekha kudzera m’malamulo. God ndiye Mzimu. Ndipo kodi ife timatcha chiyani Baibulo? Ife timatcha ilo Mau a God.
Kwanenedwa apa kuti, “Musiya lamulo la God, nimusunga mwambo wa anthu.” Pali ndime 613 ku Lamulo Wake. Chitani ichi koma osachita icho; lemekezani makolo anu, ndi zina zotero. Mu Levitiko, mukunena kuti akazi ayenera kuchita zotero ndipo amuna ayenera kuchita zotero komanso zochita pamene nyama yoweta yagwera m’mbuna, ndi zina zotero. Muli ndime 613 zotero, Lamulo Wake.
Koma chifukwa chakuti iwo si mau a munthu, tiyenera kuwaganizira mobwerezabwereza. Ife tiyenera kumvera God ndipo ngakhale ndife olephera kusunga onse a Malamulo Wake, ife mosachepera tiyenera kuwazindikira iwo.
Kodi pali Mau amodzi a God amene si olondola? Afarisi anaika pambali malamulo a God. Iwo ankasunga mwambo wa anthu kuposa malamulo Wake. Mau a akuluakulu ao ankalememera kwambiri kuposa Mau a God. Zinali choncho pamene Yesu anabadwa. Yesu anadana nazo kwambiri pamene anthu sanazindikire Mau a God.
God watipatsa ife ndime 613 za Lamulo kuti atiphunzitse ife kuti Iye ndi Choonadi, Iye ndi God wathu, kuti machimo athu ndichani pamaso Wake, komanso kuti atisonyeze ife Chiyero Wake. Choncho, chifukwa chakuti ndife tonse ochimwa pamaso Wake, ife tiyenera kukhulupilira mwa Yesu amene anatumidwa kwa ife kuchokera kwa God chifukwa cha chikondi Wake pa ife ndipo ife tiyenera kukhala ndi moyo mwa chikhulupiriro.
Iwo amene amaika pambali Mau Wake, komanso iwo amene sakhulupirira ndi ochimwa. Iwo amene ndi olephera kusunga Mau Wake ndi ochimwanso, koma ndi tchimo lapamwamba kuika pambali Mau Wake. Iwowo ndi amene adzakathera ku Gahena. Kusakhulupilira ndiko kuchimwa pamaso Wake.
 
 

Chifukwa Chimene God Anatipatsira Ife Lamulo

 

Kodi ndi chifukwa chiyani God anatipatsa ife Lamulo?
Kutithandiza kuzindikira machimo athu ndi chilango chawo
 
Kodi ndi chifukwa chiti chimene God anatipatsira ife Lamulo? Kuti tizindikire machimo athu ndi kubwerera m’manja Mwake. Iye anatipatsa ife ndime 613 za Lamulo kuti tizindikire machimo athu ndi kuomboledwa kudzera mwa Yesu. Ichi ndi chifukwa chake God anatipatsa ife Lamulo. 
Kwanenedwa mu Aroma 3:20 kuti, “Pakuti uchimo udziwika ndi lamulo.” Choncho ife tikudziwa kuti chifukwa chimene God anatipatsira ife Lamulo sikutikakamiza ife kuti tikhale mwa ilo.
Ndiye kodi ndi chidziwitso chanji chimene ife timapeza ku Lamulo? Ndikuti ndife ofooka kwambiri moti sitingathe kumvera Chilamulo chonse ndi kuti ndife ochimwa pamaso Wake. Ndipo kodi ife timazindikira chiyani ku ndime 613 za Lamulo Wake? Ife timazindikira zoperewera zathu, kulephera kwathu kukhala mwa Lamulo Wake. Ife timazindikira kuti ife, zolengedwa za God, ndife zolengedwa zopanda mphamvu. Ife timazindikira kuti ndife ochimwa pamaso Wake, ndipo ife tiyenera tonse kuthera mu gahena malingana ndi Lamulo Wake. 
Pamene tizindikira machimo athu komanso kupanda mphamvu kwathu, ndiye timatani? Kodi ife timayesa kukhala anthu angwiro? Ayi. Chomwe ife tiyenera kuchita ndi kuvomereza kuti ndife ochimwa, kukhulupilira mwa Yesu, kuomboledwa kudzera mu chipulumutso Wake cha madzi ndi Mzimu Woyera, komanso kumuthokoza Iye. 
Chifukwa chimene Iye anatipatsa ife Lamulo ndi kutipanga ife kuzindikira machimo athu ndi zilango za machimo amenewo kuti tidziwe kuti sitingapulumutsidwe ku gahena popanda Yesu. Ngati timakhulupirira mwa Yesu ngati Mpulumutsi wathu, tidzaomboledwa. Iye anatipatsa ife Lamulo kuti atipulumutse.
Iye anatipatsa ife Lamulo kuti atipange ife kuzindikira momwe tilili ochimwa kwathunthu ndi kupulumutsa miyoyo yathu ku uchimo. Iye anatipatsa ife Lamulo ndipo anatuma Yesu kudzatipulumutsa. God anatuma mwana Wake mwini kuti atenge machimo athu kudzera mu ubatizo Wake. Ndipo tikhoza kupulumutsidwa pokhulupirira Iye.
Ife tiyenera kuzindikira kuti ndife ochimwa opanda chiyembekezo ndipo tiyenera kukhulupirira mwa Yesu kuti ife timasulidwe ku uchimo, kukhala ana Wake ndi kubweza ulemerero kwa God. 
Ife tiyenera kumvetsetsa Mau Wake. Chiyambi chonse ndi chochokera kwa Iye. Ife tiyeneranso kuyamba ndi Mau Wake ndi kumvetsetsa choonadi cha chiombolo kudzera m’Mau Wake. Ife tiyenera kuganiza komanso kuweruza kudzera m’Mau Wake. Ichi ndi chikhulupiriro cholondola ndi chowona.
 
 
Kodi ndi Chiyani Chomwe Chili mu Mtima wa Munthu?
 
Kodi ife tiyenera kuchita chiyani pamaso pa God?
Ife tiyenera kuvomereza machimo athu ndi kupempha God kuti atipulumutse ife.
 
Chikhulupiriro chiyenera kuyamba ndi Mau a God, ndipo ife tiyenera kukhulupilira mwa God kudzera m’Mau Wake. Ngati sititero, tidzagwa mu cholakwa. Icho chidzakhala chikhulupiriro cholakwika komanso chabodza.
Pamene Afarisi ndi alembo anaona ophunzira a Yesu akudya mkate osasamba m’manja, iwo sakanatha kudzudzula iwo ngati iwo akadaona icho kudzera m’Mau a God. Mau akuti chilichonse chomwe chimalowa mwa munthu kuchokera kunja sichingadetse chifukwa chimapita m’mimba mwake, osati m’mtima mwake, ndipo chimatuluka kunja.
Monga kwanenedwa mu Marko 7:20-23 kuti, “Ndipo anati, Chotuluka mwa munthu ndicho chidetsa munthu. Pakuti m’kati mwake mwa mitima ya anthu, mutuluka maganizo oipa, zachiwerewere, zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa: zoipa izi zonse zituluka m’kati, nkudetsa munthu.” Yesu ananena kuti anthu ndi ochimwa chifukwa chakuti iwo amabadwa ndi uchimo.
Kodi inu mukumvetsetsa zomwe zimenezi zikutanthauza? Ife timabadwa monga ochimwa chifukwa chakuti ndife tonse mbadwa za Adamu. Koma ife sitingaone choonadi chifukwa chakuti ife sitivomera ngakhalenso kukhulupilira m’Mau Wake onse. Kodi ndi chiyani chili m’kati mwa mtima wa munthu?
Tiyeni tione pa Marko 7:21-22. “Pakuti m’kati mwake mwa mitima ya anthu, mutuluka maganizo oipa, zachiwerewere, zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa: zoipa izi zonse zituluka m’kati, nkudetsa munthu.” Zonse zimenezi zimaturuka m’kati mwa mtima wa munthu ndi kumudetsa iye komanso ena.
Kwalembedwa mu Masalmo kuti, “Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika, munthu ndani kuti mumkumbukira? (Ndi mwana wa munthu kuti mumuchezera?—NKJV)” (Masalimo 8:3-4).
Ndi chifukwa chiyani Iye amatichezera? Iye amatichezera chifukwa amatikonda. Iye anatilenga ife, anatikonda, ndipo anachita chifundo pa ife ochimwa. Iye anafafaniza machimo athu onse ndipo anatipanga ife kukhala anthu Wake. “Yehova, Ambuye wathu, dzina lanu liposadi nanga padziko lonse lapansi! Inu amene munaika ulemerero wanu pa thambo la kumwamba.” (Masalimo 8:1) Mfumu Davide anaimba m’Chipangano Chakale pamene iye anazindikira kuti God adzakhala Mpulumutsi wa ochimwa.
Mu Chipangano Chatsopano, mtumwi Paulo ananena chinthu chomwecho. Ndi chinthu chodabwitsa kuti ife, zolengedwa za God, tingakhale ana Wake. Zimatheka kokha kupyolera mu chifundo Wake kwa ife. Ichi ndi chikondi cha God.
Kuyesa kukhala moyo mwa Lamulo la God kwathunthu ndi, mwanjira ina, kutsutsa ndi God. Ndipo ndi lingalironso limene limaturuka chifukwa cha umbuli wathu. Si bwino kukhala kunja kwa chikondi Wake polimbana ndi kusunga Lamulo komanso kupemphera. Ndi chifuniro cha God kuti ife tiyenera kuzindikira kuti ndife ochimwa kudzera mu Lamulo ndi kukhulupilira mu chiombolo cha madzi ndi mwazi (Mzimu Woyera).
Mau Wake alembedwa mu Marko 7:20-23 kuti, “Chotuluka mwa munthu ndicho chidetsa munthu. Pakuti m’kati mwake mwa mitima ya anthu, mutuluka maganizo oipa, zachiwerewere, zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa: zoipa izi zonse zituluka m’kati, nkudetsa munthu.”
Yesu ananena kuti choturuka mwa anthu, machimo mkati, amadetsa iwo. Chakudya chimene God amatipatsa ife sichingadetse anthu. Zolengedwa zonse ndi zoyera, koma zotuluka mwa munthu, ndizo machimo ake, ndizo zimamudetsa. Tonsefe timabadwa mbadwa za Adamu. Ndiye kodi ife timabadwa bwanji? Ife timabadwa ndi mitundu khumi ndi iwiri ya machimo.
Ndiye, kodi ife tingakhale opanda uchimo? Ife tidzapitiriza kuchimwa, pakuti ife tinabadwa ndi uchimo. Kodi ife tingasiye tokha kuchimwa chifukwa chabe chakuti ife timadziwa Lamulo? Kodi tingathe kukhala moyo molingana ndi malamulo? Ayi.
Pamene tikuyesera kwambiri, ndi pamenenso zimavuta kwambiri. Tiyenera kuzindikira malire athu ndi kupereka. Kenako, ndi maganizo odzichepetsa, ife tingavomere ubatizo ndi mwazi wa Yesu, zimene zimatipulutsa ife.
Nkhani zonse zokwana 613 za m’Chilamulo ndi zolondola komanso zachilungamo. Koma anthu ndi ochimwa kuyambira nthawi yomwe anapangidwa m’mimba mwa amayi awo. Pamene ife tazindikira kuti Lamulo la God ndi cholondola koma kuti ife timabadwa ochimwa amene sitingakhale konse olungama mwa ife tokha, ife timazindikiranso kuti tikufunika chifundo cha God komanso tikufunika kupulumutsidwa ndi chiombolo cha Yesu m’madzi, mwazi, ndi Mzimu Woyera. Pamene ife tazindikira malire athu, kuti ife sitingakhale olungama mwa ife tokha ndipo ife tidzapita ku gahena chifukwa cha machimo athu, ife sitingakwanitse koma kudalira pa chiombolo cha Yesu. 
Tiyenera kudziwa kuti sitingakhale olungama kapena abwino pamaso pa God mwa ife tokha. Choncho, tiyenera kuvomereza pamaso pa God kuti ndife ochimwa amene amayenera kupita ku gehena, ndipo tingapemphere chifundo Wake, “God, chonde ndipulumutseni ku machimo anga ndipo mundichitire chifundo.” Ndiye, God ndithudi adzakomana nafe mu Mawu Wake. Motere, ife tingapulumutsidwe.
Ife timakonda kuona pemphero la Davide ngati Mau olembedwa a God. “kuti mukhale wolungama pakulankhula Inu, mukhalenso woyera pa kuweruza kwanu.” (Masalimo 51:4)
Davide ankadziwa kuti iye anali mulu wa uchimo amene anali woipa mokwanira kuponyedwa mu gahena koma iye anavomereza icho pamaso pa God. “Ngati Inu munditcha ine wochimwa, ndine wochimwa; Ngati Inu munditcha ine wolungama, ndine wolungama; Ngati Inu mundipulumutsa in, ndidzapulumuka; ndipo ngati Inu mundipititsa ine ku gahena, ine ndidzathera mu gahena.”
Ichi ndi chikhulupiriro cholondola. Umu ndi momwe timapulumutsidwira. Umu ndi mmene tiyenera kukhala ngati tikuyembekeza kukhala okonzeka kukhulupirira chiombolo cha Yesu.
 
 

Ife Tiyenera Kudziwa Ndendende Kuti Machimo Athu Ndichani 

 
Popeza tonse ndife mbadwa za Adamu, ife tonse tili ndi chilakolako mmitima yathu. Komabe, kodi God amatiuza chiyani ife? Iye amatiuza ife kuti tisachite chigololo. Tili ndi kupha m’mitima mwathu, koma kodi God amatiuza ife chiyani? Iye amatiuza ife kuti tisaphe. Ife tonse timanyoza makolo athu m’mitima yathu, koma Iye amatiuza ife kulemekeza makolo athu. Ife tiyenera kuzindikira kuti Mau Wake onse ndi abwino komanso kuti ife tonse tili ndi machimo m’mitima yathu.
Kodi izi ndi zolondola kapena ayi? Ndi zolondola mwamtheradi. Choncho, kodi ife tiyenera kuchita chiyani pamaso pa God? Ife tiyenera kuvomereza kuti ndife mulu wa uchimo, ochimwa opanda chiyembekezo. Si bwino kuganiza kuti ife tinali olungama dzulo chifukwa chakuti ife tinachina ntchito zabwino ndipo ochimwa lero chifukwa chakuti ife tachita machimo lero. Ife timabadwa ochimwa. Chilichonse chimene ife timachita, ife tidzakhalabe ochimwa. Ichi ndi chifukwa chake ife tiyenera kuomboledwa kudzera m’madzi ndi mwazi wa Yesu. 
Si ndife ochimwa chifukwa cha ntchito zathu, monga kuchita chigololo, kupha, kuba, ndi zina zotero, koma ndife ochimwa chifukwa chakuti ife tinabadwa monga ochimwa. Ife tinabadwa ndi mitundu khumi ndi iwiri ya machimo. Chifukwa chakuti ife tinabadwa ochimwa m’maso mwa God, ife sitingakhale konse abwino mwa mphamvu zathu. Ife tinganamizira kokha kukhala abwino.
Ife timabadwa ndi malingaliro odzadza ndi machimo monga kupha, kuba, ndi zina zotero. Choncho, kodi ife tingakhale bwanji olungama chifukwa chokha chakuti ife kwenikweni sitichita machimo amenewa? Ife sitingakhale olungama pamaso pa God mwa ife tokha. Ngati ife timanena kukhala olungama, ndi chinyengo. Yesu anatcha Afarisi ndi alembi ‘Afarisi ndi alembi achinyengo’. Anthu amabadwa ochimwa. Iwo amachimwa pamaso pa God m’miyoyo yao yonse.
Aliyense onena kuti iye sanamenyepo kapena kugunda winawake kapena kuba ngakhale singano kwa winawake m’moyo wake onse akunama chifukwa chakuti anthu amabadwa monga ochimwa. Munthu ameneyo ndi wabodza, wochimwa, komanso wachinyengo. Umu ndi momwe God amaonera iwo.
Ndinu obadwa ochimwa. Ngakhale inu simuchita mchitidwe umodzi wa uchimo, inu mukupita ku gahena. Ngakhale inu kwenikweni mutasunga Lamulo komanso ambiri a malamulo, inu mudzakhalabe ochimwa opangidwiratu kupita ku gahena.
Ndiye kodi ife tiyenera kuchita chiyani pamaso pa tsogolo lotero? Ife tiyenera kupempherera chifundo Wake ndi kudalira pa Iye kuti tipulumutsidwe ku machimo athu. Ngati Iye satipulumutsa ife, ife sitingakwanitse koma kupita ku gahena. Ili ndi tsogolo lathu.
Iwo amene amavomera Mau Wake amavomerezanso kuti iwo indedi ndi ochimwa. Ndipo iwo amadziwanso kuti iwo ndi olungama. Choncho, iwo amadziwa kuti kuika pambali Mau Wake popanda kuzindikira Mau Wake ndi tchimo. Iwo amene amavomera Mau Wake ndi olungama ngakhale iwo anali ochimwa m’mbuyo. Iwo ndi obadwa mwatsopano ndi Mau Wake ndi kulandira chisomo Wake. Iwo ndiwo odalitsidwa kwambiri.
 
 
Iwo Amene Amayesa Kuomboledwa kudzera mu Ntchito Zao Ndi Ochimwabe
 
Kodi ndani amene adakali ochimwa ngakhale pamene iwo akhulupilira mwa Yesu?
Iwo amene amayesa kuomboledwa kudzera mu ntchito zao
 
Tiyeni tione pa Agalatiya 3:10 ndi 11. “Pakuti onse amene ali a ntchito za lamulo ali pansi pa temberero; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa aliyense wosapitiriza m’zonse zolembedwa m’buku la chilamulo, kuzichita izi. Koma kuti palibe munthu ayesedwa wolungama ndi lamulo pamaso pa Mulungu(God) ndi zooneka, pakuti wolungama adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro—NKJV.”
Zimanenedwa kuti aliyense wosapitiriza m’zonse zolembedwa m’buku la chilamulo ndi wotembereredwa. Iwo amene amakhulupilira mwa Yesu koma kuyesa kulungamitsidwa ndi ntchito zao ndi otembereredwa. Kodi ali kuti iwo amene akuyesa kulungamitsidwa ndi ntchito zao? Iwo ali pansi pa temberero la God.
Kodi ndi chifukwa chiyani God anatipatsa ife Lamulo? Iye anatipatsa ife Lamulo kuti ife tizindikire machimo athu (Aroma 3:20). Kuti ife tizindikire kuti ndife ochimwa otheratu komanso ndife oikidwira kupita ku gahena.
Khulupirirani mu ubatizo wa Yesu, Mwana wa God, ndipo mubadwenso mwatsopano ndi madzi ndi Mzimu Woyera. Kenako inu mudzapulumutsidwa ku machimo anu, kukhala wolungama, kukhala ndi moyo wamuyaya, ndi kupita kumwamba. Khalani ndi chikhulupiriro m’mitima yanu.
 
 
Tchimo Lodzikuza Kwambiri pa Dziko Lapansi 
 
Kodi tchimo lodzikuza kwambiri pa dziko lapansi ndi chiyani?
Kuyesa kukhala moyo potsata Lamulo
 
Palibe chofunika kwambiri kuposa kukhulupilira mwa God. Ndife odalitsidwa pokhala ndi chikhulupiriro mu dalitso Wake. God anatsimikiza kupulumutsa iwo amene ali ndi chikhulupiriro mu Mau Wake.
Koma lero, mwa okhulupirira, pali ambiri amene amayesa kukhala mwa Lamulo Wake. Akristu ambiri ali otero. N’zoyamikirika kuti amayesetsa kutsatira Chilamulo, koma zingatheke bwanji?
Tiyenera kuzindikira kuti ndi kopusa bwanji kuyesa kukhala moyo molingana ndi Lamulo Wake. Pamene tikuyesera kwambiri, zimakhala zovuta kwambiri. Iye anati, “Chikhulupiriro chidza mwa kumva, ndi kumva kudza mwa mau a Khristu—NKJV.” (Aroma 10:17) Tiyenera kutaya kudzikuza kwathu kuti tipulumutsidwe.
 
 

Ife Tiyenera Kusiya Miyezo Yathu kuti Tipulumutsidwe 

 
Kodi ife tiyenera kuchita chiyani kuti tipulumutsidwe 
Ife tiyenera kusiya miyezo yathu
 
Kodi munthu angapulumutsidwe bwanji? Ndi zotheka kokha pamene iwo azizindikira okha kukhala ochimwa. Pali ambiri amene sanapulumutsidwe chifukwa chakuti iwo sangasiye zikhulupiliro zao zolakwika komanso khama. 
God ananena kuti iwo amene amagwiritsitsa ku Lamulo ndi Wotembereredwa. Iwo amene amakhulupilira kuti angakhale wolungama pang’ono pang’ono pamene iwo akupitiriza kukhulupilira mwa Yesu komanso kuyesa kukhala mwa Lamulo ali pansi pa temberero Wake. Iwo amakhulupilira mwa God, koma iwo amaganizabe kuti iwo ayenera kukhala malingana ndi Lamulo kuti apulumutsidwe.
Okondedwa nzanga, kodi ife tingakhale olungama kudzera mu ntchito zathu pamene ife tidakali ndi moyo? Ife timakhala olungama pokhulupirira kokha m’Mau a Yesu, ndipo pokhapo ndi pamene ife timaomboledwa. Pokhala kokha ndi chikhulupiriro mu ubatizo wa Yesu, mwazi Wake, ndi Yesu kukhala God, ife taomboledwa.
Icho ndi chifukwa chake God anakonza lamulo la chikhulupiriro kwa ife monga njira yokhalira wolungama. Chiombolo cha madzi ndi Mzimu Woyera sichigona mu ntchito za anthu koma mu chikhulupiriro m’Mau a God. Ndipo God anatipulumutsa ife chifukwa cha chikhulupiriro chimenecho. Umo ndi momwe God anakonzera icho komanso momwe Iye anatsirizira icho.
Kodi ndi chifukwa chiyani iwo amene anakhulupirira mwa Yesu sanaomboledwe? Chifukwa chakuti iwo sanavomere mau a chiombolo a madzi ndi Mzimu Woyera. Koma ife, amene ndife opanda ungwiro monga momwe alili, taomboledwa chifukwa cha chikhulupiriro chathu m’mau a God.
“awiri adzakhala opera pamphero; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa.” (Mateyu 24:41) Mmodzi amene wasiyidwa ndi iye amene sanaomboledwe. Kodi ndi chifukwa chiyani mmodzi adzatengedwa ndi wina adzasiyidwa?
Chifukwa ndi chakuti mmodzi anamvera ndi kukhulupilira m’mau a God. Wina amene analimbikira kusunga Lamulo pamapeto pake anaponyedwa ku gahena. Iye ankayesa kukwawira kwa God, koma God adamusasa iye monga momwe ife timasasira nyerere pamene iyo ikuyesa kukwawira mwendo wathu. Ngati munthu akuyesa kukwawira kwa God poyesa kusunga Lamulo, iye ndithudi adzaponyedwa mu gahena.
Icho ndi chifukwa chake ife tiyenera kuomboledwa ndi chikhulupiriro m’madzi ndi Mzimu Woyera.
“Pakuti onse amene ali a ntchito za lamulo ali pansi pa temberero; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa aliyense wosapitiriza m’zonse zolembedwa m’buku la chilamulo, kuzichita izi. Koma kuti palibe munthu ayesedwa wolungama ndi lamulo pamaso pa Mulungu(God) ndi zooneka, pakuti wolungama adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro —NKJV.” (Agalatia 3:10-11, Aroma 1:17)
Kusakhulupilira m’Mau a God ndi tchimo pamaso pa God. Kuonjezera apo, ndi tchimonso kuika pambali Mau a God malingana ndi muyezo wa munthu. Ife anthu sitingakhale mwa Lamulo Wake chifukwa chakuti ife tonse timabadwa ochimwa. Ndipo ife timapitiriza kuchimwa miyoyo yathu yonse. Ife timachimwa pang’ono pano, pang’ono apo, komanso paliponse pamene ife timapita. Tiyenera kuzindikira kuti thupi lathu silingachitire mwina koma kuchimwa.
Munthu ali ngati chidebe chachikuru cha ndowe. Ngati ife tayesa kunyamula icho mozungulira, ife timamwaza zomwe zili mkati mwa njira yonse. Ife tili monga choncho. Ife timapitiriza kumwaza uchimo kulikonse kumene ife timapita. Kodi inu mukuona icho?
Kodi inu mukanali kupitiriza kudzinyenga kuti ndinu woyera? Ngati mukanatha kudziona bwino lomwe, mukanasiya kuyesera pachabe kukhala woyera ndipo mukanakhulupirira madzi ndi magazi a Yesu.
Ife tikufunika kuchotsa kuuma khosi kwathu ndi kuvomereza kuti ndife ochimwa pamaso pa God. Kenako, ife tiyenera kubwerera ku Mau Wake ndi kupeza momwe Iye anawapulumutsira iwo ndi madzi ndi Mzimu Woyera.
 
Ulaliki uwu ukupezekanso mu mtundu wa ebook. Dinani pachikuto cha buku pansipa.
KODI MWABADWADI MWATSOPANO MWA MADZI NDI MZIMU WOYERA? [Kusindikiza Kokonzedwanso Kwatsopano]