• All e-books and audiobooks on The New Life Mission website are free
  • Explore multilingual sermons in global languages
  • Two new revised editions in English have been released
  • Check out our website translated into 27 languages
Search

Sermons

Mutu 2: Lamulo

[2-1] Ngati Ife Tichita Zinthu Motsatira Lamulo, Kodi Ilo Lingatipulutse Ife? (Luka 10:25-30)

Ngati Ife Tichita Zinthu Motsatira Lamulo, Kodi Ilo Lingatipulutse Ife? (Luka 10:25-30)
(Luka 10:25-30)
“Ndipo taonani, wachilamulo wina anaimirira namuyesa Iye, nanena, Mphunzitsi, ndidzalowa moyo wosatha ndi kuchita chiyani? Ndipo anati kwa iye, M’chilamulo mulembedwa chiyani? Uwerenga bwanji? Ndipo iye anayankha nati, Uzikonda Ambuye Mulungu(God) wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi (maganizo—NKJV) zako zonse, ndi mnansi wako monga iwe mwini. Ndipo anati kwa iye, Wayankha bwino; chita ichi, ndipo udzakhala ndi moyo. Koma iye, pofuna kudziyesa yekha wolungama, anati kwa Yesu, Ndipo mnansi wanga ndani’ Ndipo Yesu anamlanda mau, nati, Munthu wina anatsika kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Yeriko; ndipo anagwa m’manja a achifwamba amene anamvula zovala, namkwapula, nachoka atamsiya wofuna kufa.” 
 
 
Kodi vuto lalikulu la munthu ndi chiyani?
Amakhala ndi mafantasi ambiri olakwika.
 
Luka 10:28, “Chita ichi, ndipo udzakhala ndi moyo.”
Anthu amakhala ndi mafantasi ambiri olakwika. Zikuoneka kuti iwo ali pachiwopsezo makamaka pankhaniyi. Iwo amaoneka kukhala anzeru koma amanyengedwa mosavuta ndi kukhalabe osadziwa za mbali zao zoipa. Timabadwa osadziwa tokha, koma timakhalabe ngati tikudziwa. Chifukwa anthu sadziwa okha, Baibulo limati ndife ochimwa.
Anthu amakamba za kukhalapo kwa machimo ao. Ndipo iwo ndi osakhoza kuchita zabwino, komabe iwo amakonda kwambiri kudzifotokoza okha monga abwino. Iwo amafuna kudzitamandira za ntchito zao zabwino ndi kudzionetsera. Iwo amanena kuti ndi ochimwa koma amachita ngati kuti iwo ndi abwino kwambiri.
Iwo amadziwa kuti alibe chabwino mwa iwo ngakhalenso kuthekera kochita bwino koma iwo amayesa kunyenga ena ndipo nthawi zina ngakhale kudzinyenga okha. “Inu, ife sitingakhaliretu oipa. Muli china chake chabwino m’kati mwa ife.” 
Choncho, iwo amayang’ana ena ndi kudziuza okha kuti, “Kalanga, ndikadakonda ngati iye sadachite icho. Zikanakhala bwino kwa iye ngati iye sadachite. Iye akanakhala bwino ngati akanalankhula ngati chonchi. Ndikuganiza kuti ndi bwino kulalikira uthenga wabwino mu njira yotero ndi yotero. Iye anaomboledwa ine ndisanaomboledwa, choncho ndikuganiza kuti iye ayenera kuchita bwino kwambiri monga munthu amene waomboledwa. Ndangoomboledwa posachedwapa, koma ngati ndingaphunzire zambiri, ndidzachita bwino kwambiri kuposa momwe iye amachitira.”
Iwo akunola mipeni mu mtima mwao. “Embekezani. Inu mudzaona kuti si ndili ngati inu. Choncho inu mukuganiza kuti muli patsogolo panga tsopano, sichoncho? Embekezani. Kwalembedwa m’Baibulo kuti wotsiriza adzakhala woyaba. Ndikudziwa akutanthauza ine. Embekezani, ndipo ndidzakuonetsani.” Anthu amadzinyenga okha.
Ngakhale iye akanachita zithu mofanana ngati iye akanakhala m’malo mwa munthuyo, iye akanamuweruzabe iye.
Pamene afunsidwa ngati anthu ali ndi kuthekera kochita bwino, anthu ambiri amanena kuti iwo alibe. Koma iwo ali ndi chinyengo lakuti iwo eni ali ndi kuthekera. Choncho iwo amayesa kwambiri mpaka iwo kufa.
Iwo amaganiza kuti ali ndi ‘ubwino’ m’mitima mwao, kuti iwo ali ndi kuthekera kochita bwino. Iwo amaganizanso kuti iwo eni ndi abwino mokwanira. Mosasamala kanthu kuti ndi kwa nthawi yaitali bwanji pamene iwo anabadwa mwatsopano, ngakhale iwo amene adakwaniritsa kupita patsogolo kwakukuru mu utumiki wa God amaganiza kuti, ‘Ndingachitire ichi ndi icho Ambuye’.
Koma ngati tichotsa Ambuye wathu m’miyoyo yathu, kodi tingachitedi zabwino? Kodi pali zabwino mu umunthu? Kodi angakhale ndi moyo akuchita ntchito zabwino? Anthu alibe kuthekera kochita zabwino. Nthawi zonse pamene anthu akuyesa kuchita china chake pa iwo okha, iwo amachimwa.
Ena amakankhira Yesu pambali ataomboledwa ndi kuyesa kuchita zabwino paokha. Palibe china koma choipa mwa ife tonse. Ife tingachite kokha zoipa. Mwa tokha (ngakhale amene apulumutsidwa), tingachimwe chabe. Ndi zenizeni za thupi lathu.
 
Kodi ife nthawi zonse timachita chiyani, zabwino kapena zoipa?
Zoipa
 
M’buku lathu la matamando lotchedwa, ‘Tamandani Ambuye’, muli nyimbo yomwe imaimbidwa motere, “♪Thupi lopanda phindu limene limalakwitsa popanda Yesu, popanda inu ndili ngati sitima yopanda matanga yoyenda pa nyanja♪.” Popanda Yesu ife tingachimwe chabe. Ndife olungama chifukwa chokha chakuti ife tapulumutsidwa. Mu zoona zake, ndife oipa.
Mtumwi Paulo ananena kuti, “Pakuti chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choipa chimene sindichifuna, chimenecho ndichichita.” (Aroma 7:19) Koma ngati munthu ali ndi Yesu, izo zilibe kanthu. Koma pamene iye alibe chochita ndi Iye, iye amayesa kuchita chabwino pamaso pa God. Koma pamene iye akuyesa kwambiri, ndi pamenenso iye amadzipeza yekha akuchita zoipa.
Ngakhale Mfumu Davide anali ndi chikhalidwe chomwecho. Pamene dziko lake linali lamtendere ndi lotukuka, madzulo ena, iye anakwera padenga kukayenda. Anaona chithunzi chokopa ndipo anagwa chifukwa cha zosangalatsa zakuthupi. Kodi iye anali otani pamene iye anaiwala Ambuye! Iye anali woipa. Iye anapha Uriya ndi kutenga mkazi wake koma iye sanaone kuipa mwa iye. Iye anapanga zifukwa za machitidwe ake.
Kenako tsiku lina, mneneri Natani anadza kwa iye ndi kunena. “Mu mzinda wina munali anthu awiri; wina wolemera, wina wosauka. Wolemerayo anali nazo zoweta zazing’ono ndi zazikulu zambiri ndithu; koma wosaukayo analibe kanthu kena koma kamwana kakakazi ka nkhosa, kamene anakagula ndi kukaweta; ndipo kameneko kanakula naye pamodzi ndi ana ake. Kanadyako chakudya chake cha iye yekha, kanamwera m’chikho cha iye yekha, kanagona pa chifukato chake, ndipo kanali kwa iye ngati mwana wake wamkazi. Ndipo kwa wolemerayo kunafika mlendo, ndipo iye analeka kutengako mwa zoweta zake zazing’ono ndi zazikulu, kuphikira mlendo amene anafika kwa iye, koma anatenga mwanawankhosa wa wosaukayo, naphikira munthu amene anafika kwa iye.” (2 Samuele 12:1-4)
Davide ananena kuti, “Munthu amene anachita ichi, ayenera kumupha!” Mkwiyo wake unayaka kwambiri, choncho iye ananena kuti, “Iye ali nazo zake zambiri, iye ndithudi akanatenga imodzi pa izo. Koma iye anatenga mwana wa nkhosa yekhayo wa wosauka ndi kuphikira mlendo wake. Iye ayenera kufa!” Ndipo Natani anamuuza iye kuti, “Munthuyo ndi inu nomwe!” Ngati ife sititsata Yesu komanso osakhala ndi Iye, ngakhale obadwa mwatsopano angakhale monga choncho.
Ndi chimodzimodzi kwa amuna onse, ngakhale okhulupirika. Ife nthawi zonse timagwa, kuchita zoipa popanda Yesu. Choncho ndife othokozanso lero kuti Yesu anatipulumutsa ife mosasamala kanthu za zoipa mwa ife. “♪ Ndikufuna ndi pumule pansi pa mthunzi wa Mtanda.♪” Mitima yathu imapumula pansi pa mthunzi wa chiombolo cha Kristu. Koma ngati ife tisiya mthunzi ndi kudziyang’ana tokha, ife sitingapumule.
 
 

God Anatipatsa Ife Chilungamo cha Chikhulupiriro Asanatipatse Lamulo 

 
Kodi choyamba ndi chiti, chikhulupiriro kapena Lamulo?
Chikhulupiriro 
 
Mtumwi Paulo ananena kuti God anatipatsa ife chilungamo cha chikhulupiriro choyamba. Chilungamo cha chikhulupiriro chinadza poyamba. Iye anapereka icho kwa Adamu ndi Hava, kwa Abele, kenako kwa Seti ndi Enoke... kutsikira kwa Nowa..., kenako kwa Abrahamu, kenako kutsikira kwa Isake, kwa Yakobo ndi ana ake khumi ndi awiri. Ngakhale popanda lamulo iwo anakhala olungama pamaso pa God kudzera mu chikhulupiliro chao m’Mawu Wake. Iwo anadalitsidwa ndi kupatsidwa mpumulo kudzera mu chikhulupiliro chao m’Mawu Wake.
Ndipo nthawi inapita ndipo mbadwa za Yakobo zinakhala mu Aigupto monga akapolo kwa zaka 400 chifukwa cha Yosefe. Kenako God anawaturutsa iwo kudzera mwa Mose kupita mu mzinda wa Kanani. Komabe, m’zaka 400 za ukapolo, iwo adaiwala chilungamo cha chikhulupiriro.
Choncho God anawaolotsa iwo Nyanja Yofiira kudzera mu chozizwa Chake ndi kuwatsogolera iwo m’chipululu. Pamene iwo anafika ku chipululu cha Sini, Iye anawapatsa Lamulo pa Phiri la Sinai. Iye anawapatsa Malamulo Khumi, amene anali ndi mfundo 613 zatsatanetsatane za Lamulo. “Ine ndine Yehova God wanu, God wa Abrahamu, God wa Isaki, God wa Yakobo. Mulole Mose akwere ku Phiri la Sinai, ndipo ndidzakupatsani lamulo.” God anapatsa Israeli Lamulo.
Iye anawapatsa iwo Lamulo kuti iwo akhale ndi ‘uchimo udziwika’ (Aroma 3:20). Kunali kuwalola iwo kuti adziwe zomwe God ankakonda komanso zomwe Iye sankakonda ndi kuvumbulutsa chilungamo Wake komanso chiyero.
Anthu onse a Israeli amene anali akapolo mu Aigupto kwa zaka 400 anaoloka Nyanja Yofiira. Iwo anali asadakumanepo ndi God wa Abrahamu, God wa Isake, God wa Yakobo. Iwo sanamudziwe Iye.
Ndipo pamene iwo ankakhala monga akapolo kwa zaka 400, iwo adaiwala chilungamo cha God. Pa nthawi imeneyo, iwo analibe mtsogoleri. Yakobo ndi Yosefe anali atsogoleri ao, koma iwo adafa. Zikuoneka kuti Yosefe analephera kupereka chikhulupiriro kwa ana ake, Manase ndi Efraimu.
Choncho anafunika kupezanso God wawo ndi kukumana naye chifukwa anali atayiwala chilungamo cha God. Choncho God anawapatsa iwo chilungamo cha chikhulupiriro choyamba ndipo kenako kuwapatsa iwo Lamulo pamene iwo adaiwala chikhulupiriro. God anawapatsa iwo Lamulo kuti awabweze iwo kwa Iye.
Kuti apulumutse Israeli, kuti apange iwo kukhala anthu Wake, anthu a Abrahamu, Iye anawauza iwo kuti adulidwe.
Cholinga Wake mu kuitana iwo chinali kuti choyamba awadziwitse iwo kuti kuli God pokhazikitsa Lamulo ndipo cha chiwiri kuwadziwitsa kuti iwo anali ochimwa pamaso Wake. Iye ankafuna kuti iwo adze pamaso Wake ndi kukhala anthu Wake powaombola kudzera mu nsembe ya chiombolo imene God anawapatsa. Ndipo Iye anawapanga iwo anthu Wake.
Anthu a Israeli anaomboledwa kudzera mu lamulo (ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe) pokhulupilira mwa Mesiya amene amadza. Koma ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe inazimiririka popita pa nthawi. Tiyeni tione kuti nthawi imeneyo inali iti. 
Mu Luka 10:25, “Wachilamulo wina anaimirira namuyesa Iye.” Wachilamuloyu anali Mfalisi. Afarisi anali anthu osamala amene anayesa kukhala mwa Mawu Wake. Iwo anali anthu amene anayesa kuteteza dziko choyamba ndipo kenako kukhala motsatila Lamulo Wake. Ndipo kenako kunali Achangu amene anali opupuluma kwambiri komanso okonda kupita ku ziwonetsero kuti akwaniritse masomphenya awo.
 
Kodi Yesu amafuna kukumana ndi ndani?
Ochimwa opanda Mbusa
 
Pali anthu ngati iwo ngakhale lero. Iwo amatsogolera mayendedwe a anthu ndi mau monga ‘Pulumutsani anthu oponderezedwa a dziko’. Iwo amakhulupilira kuti Yesu anadza kudzapulumutsa osauka komanso oponderezedwa. Chotero, amaphunzira zaumulungu m’maseminale a zaumulungu, kutengamo mbali m’zandale, ndi kuyesa ‘kupulumutsa osowa’ m’mbali iriyonse ya anthu.
Iwo ndi amene amakakamira kuti, “Tiyeni tonse tikhale Motsatira Lamulo loyera komanso la chifundo. Khalani motsatira Lamulo, motsatira Mawu Wake.” Koma iwo sazindikira tanthauzo lenileni la Lamulo. Iwo amayesa kukhala molingana ndi malemba a Lamulo koma sakuzindikira vumbulutso wopatulika la Lamulolo.
Choncho ife tinganene kuti panalibe mneneri, mtumiki wa God, pafupifupi kwa zaka 400 Kristu asanadze. Motere iwo anakhala gulu la nkhosa lopanda mbusa.
Iwo analibe Lamulo ngakhalenso mtsogoleri. God sanadzionetse Yekha kudzera mwa atsogoleri onyenga achipembedzo a nthawi imeneyo. Dziko lidakhala pansi pa ulamuliro wa Ufumu wa Chiroma. Choncho Yesu ananena kwa anthu amenewo a Israeli amene anamutsata Iye m’chipululu kuti Iye sadzawasiya iwo ndi njala. Iye anamvera chisoni nkhosa zopanda mbusa. Panali anthu ambiri amene ankavuta pa nthawi imeneyo.
Kwenikweni achilamulo ndi ena m’maudindo otero ndi amene adali ndi ufulu wopatsidwa; Afarisi anali a m’badwo wa Israeli, wa Ayuda. Iwo anali onyada kwambiri.
Ndipo wachilamulo ameneyu anafunsa Yesu mu Luka 10:25 kuti, “Ndidzalowa moyo wosatha ndi kuchita chiyani?” Zinaoneka kwa wachilamuloyu kuti kunalibe wabwino kuposa iye pakati pa anthu a Israeli. Choncho wachilamulo ameneyu (m’modzi amene adali asanaomboledwe) anamutsutsana naye, ponena kuti, “Ndidzalowa moyo wosatha ndi kuchita chiyani?”
Wachilamulo uyu ndi chithunzithunzi cha ife tokha. Iye anafunsa Yesu kuti, “Ndidzalowa moyo wosatha ndi kuchita chiyani?” Yesu ananena kwa iye kuti, “M’chilamulo mulembedwa chiyani? Uwerenga bwanji?”
Choncho iye anayankha ndi kunena kuti, “Uzikonda Ambuye Mulungu(God) wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi (maganizo—NKJV) zako zonse, ndi mnansi wako monga iwe mwini.”
Yesu anamuuza iye kuti, “Wayankha bwino; chita ichi, ndipo udzakhala ndi moyo.”
Iye anamutsutsana ndi Yesu osadziwa mwini kuti anali woipa, mulu wa uchimo amene sangachite konse chabwino. Choncho Yesu anamufunsa iye kuti, “M’chilamulo mulembedwa chiyani? Uwerenga bwanji?”
 
Kodi inu muwerenga bwanji M’cilamulo?
Ndife ochimwa amene sitingasunge konse Lamulo.
 
“Ndipo anati kwa iye, M’chilamulo mulembedwa chiyani? Uwerenga bwanji? Ndipo iye anayankha nati, Uzikonda Ambuye Mulungu(God) wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi (maganizo—NKJV) zako zonse, ndi mnansi wako monga iwe mwini. Ndipo anati kwa iye, Wayankha bwino; chita ichi, ndipo udzakhala ndi moyo.” (Luka 10:26-28)
“Uwerenga bwanji?” Zimenezi zikutanthauza momwe mumadziwira ndi kumvetsetsa Lamulo.
Monga anthu ambiri amachitira masiku ano, wachilamulo ameneyu ankaganiza kuti God anampatsa iye Lamulo kuti iye asunge. Choncho iye anayankha kuti, “Uzikonda Ambuye Mulungu(God) wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi (maganizo—NKJV) zako zonse, ndi mnansi wako monga iwe mwini.”
Lamulo linalibe chilema. Iye anatipatsa ife Lamulo langwiro. Iye anatiuza ife kuti tizikonda Ambuye ndi mtima wathu wonse ndi moyo wathu wonse, ndi mphamvu yathu yonse komanso kukonda mnansi wathu monga ife eni. Ndi cholondola kwa ife kukonda God wathu ndi mtima wathu wonse ndi mphamvu zathu, koma anali mau oyera amene sakanasungidwa konse. 
“Uwerenga bwanji?” zikutanthauza kuti Lamulo ndi cholondola komanso cholondola, koma inu mumachimvetsa bwanji? Loyayo anaganiza kuti God anaupereka kuti amvere. Koma lamulo la God linapatsidwa kuti ife tidziwe zoperewera zathu ndi kuvumbulutsa mphulupulu zathu motheratu. limavumbulutsa machimo athu kuti, “Wachimwa. Iwe unapha pamene ndinakuuza kuti usaphe. Kodi ndi chifukwa chiyani sumandimvera Ine?”
Lamulo limavumbulutsa machimo m’mitima ya anthu. Tiyeni tiyerekeze kuti poyenda munjira, ndaona mavwembe m’munda. God anandichenjeza ine ndi lamulo kuti, “Osatenga mavwembe amenewo kuti udye. Zidzandichititsa Ine manyazi ngati iwe utero.” “Inde, Atate.” “Mundawo ndi wa abambo akuti ndi akuti, choncho iwe sukuyenera kutenga iwo.” “Inde, Atate.”
Nthawi yomweyo pamene ife tamva mwa Lamulo kuti ife sitiyenera kutenga iwo, ife timamva chilakolako champhamvu chotenga iwo. Ngati ife tikanikiza spring (kapena chinthu chobwezera) pansi, icho chimakonda kutikankhanso mobwezera. Machimo a anthu ali monga choncho.
God anatiwuza ife kuti tisamachite zoipa konse. God anganene choncho chifukwa chakuti Iye woyera, chifukwa chakuti Iye ndi wangwiro, chifukwa chakuti Iye ali ndi kuthekera kochita choncho. Koma ife sitingathe ‘konse’ kusachimwa ndipo ‘sitingathe konse’ kuchita zabwino. Ife ‘sitingathe konse’ kukhala ndi zabwino m’mitima mwathu. Lamulo limanena kuti konse (linalembedwa ndi mawu oti ‘konse’). Chifukwa chiyani? Chifukwa anthu ali ndi chilakolako m’mitima mwawo. Ife timachita molingana ndi zilakolako zathu. Ife timachita chigololo chifukwa chakuti tili ndi chigololo m’mitima mwathu.
Ife tiyenera kuwerenga Baibulo mosamala. Pamene ndinakhulupilira mwa Yesu poyamba, ndinakhulupilira malingana ndi Mau. Ndinawerenga kuti Yesu anandifera ine pa Mtanda ndipo sindinathe kuletsa misozi kuyenda. Ndinali munthu woipa motero ndipo Iye anandifera ine pa Mtanda. Mtima wanga unawawa kwambiri kuti ndinakhulupilira mwa Iye. Kenako ndinaganiza kuti, ‘Ngati ndingakhulupilire ndidzakhulupilira malingana ndi Mau’.
Ndikawerenga Eksodo mutu wa 20, unanena kuti, “Usakhale nayo milungu ina koma Ine ndekha.” Ndinafufuza chikumbukiro changa kuti ndione ngati ndinayamba ndakhala nayo milungu ina pamaso Pake, kuitana dzina Lake pachabe, kapena ngati ndinayamba ndagwadirapo milungu ina. Ndinazindikira kuti ndidagwadirapo milungu ina nthawi zambiri pa nthawi ya miyambo polemekeza makolo anga. Ndidachita uchimo wokhala ndi milungu ina.
Choncho ndinapemphera molapa kuti, “Ambuye, ndapembedza mafano. Ine ndiyenera kuti ndiweruzidwe chifukwa cha izo. Chonde ndikhululukireni machimo anga. Sindidzachitanso.” Choncho tchimo limodzi linkathetsedwa.
Kenako ndinkayesa kuganiza ngati ndidaitanapo dzina Lake pachabe. Kenako ndinakumbukira kuti pamene ndinayamba kukhulupilira mwa God, ndinkasuta fodya. Anzanga ankandiuza kuti, “Kodi iwe sukuchititsa manyazi God posuta fodya? Kodi Mkristu angasute bwanji?”
Kunali kuitana dzina Wake pachabe, sichoncho? Choncho ndinapempheranso kuti, “Ambuye, ndinaitana dzina Lanu pachabe. Chonde ndikhululukireni ine. Ndisiya kusuta fodya.” Choncho ndinayesa kusiya kusuta fodya koma ndinapitiriza kuyatsa ndi kuzimitsa kwa chaka. Zinali kwenikweni zovuta kwambiri, pafupifupi zosatheka kusiya kusuta. Koma pamapeto pake, ndinakwanitsa kusiya kusuta fodya motheratu. Ndinamva kuti tchimo lina linathetsedwa.
Lotsatira linali lakuti “Udzikumbukira tsiku la Sabata, likhale lopatulika.” Ilo limatanthauza kusachita zinthu zina pa tsiku Lamlungu; osachita malonda, kapena kupeza ndalama. Choncho ndinasiyanso ilo.
Kenako kunali lakuti “Uzilemekeza atate wako ndi amai ako.” Ndinawalemekeza pamene ndinali kutali, koma anali gwero la chisoni cha mtima pamene ndinali pafupi. “Oh God wanga, ndachimwa pamaso pa God. Chonde ndikhululukireni ine, Ambuye.” Ndinapemphera molapa.
Koma sindinakwanitse kulemekeza makolo anga mopitilira chifukwa chakuti iwo onse anali atafa pa nthawi imeneyo. Kodi ndikanachita chiyani? “Ambuye, chonde khululukirani wochimwa wopanda pake ameneyu. Inu munafa pa Mtanda chifukwa cha ine.” Kodi ndinali wothokoza bwanji!
Mwanjira imeneyi, ndinaganiza kuti ndathana ndi machimo anga mmodzimmodzi. Panali malamulo ena, monga osapha, osachita chigololo, osasilira... ndinazindikira kuti sindinasunge ngakhale limodzi. Ndinapemphera usiku wonse. Koma mukudziwa, kupemphera molapa si kokoma. Tiyeni tikambe za uko.
Ndikakumbukira za kupachikidwa kwa Yesu, ndinkatha kugwirizana nazo momwe uko kunalili kopweteka kwambiri. Ndipo Iye anafa chifukwa cha ife amene sitinakwanitse kukhala moyo mogwirizana ndi mawu Wake. Ndinalira usiku wonse poganiza mmene Iye anandikondela ndipo ndinamuthokoza chifukwa chondipatsa chisangalalo chenicheni.
Chaka changa choyamba kupita ku mpingo chinali kwenikweni chophweka koma zaka zingapo zotsatira zinakhala zovuta kwambiri chifukwa chakuti ndinkayenera kuganiza kwambiri kuti misozi ituluke pakuti ndidachita choncho kawirikawiri.
Pamene misozi inkadakali osabwera, nthawi zambiri ndimapita kukapemphera m’mapiri ndi kusala kwa masiku atatu. Kenako misozi inkatuluka. Ndinkanyowa ndi misozi yanga, kubwerera ku anthu, ndi kulira mu mpingo.
Anthu ondizungulira ine ananena kuti, “Mwakhala woyera kwambiri ndi mapemphero anu m’mapiri.” Koma misozi mosalephera inkaumanso. Zinakhala zovuta kwambiri chaka chachitatu. Ndinkaganiza zoipa zimene ndidachita kwa anzanga komanso kwa Akristu anzanga ndi kuliranso. Pambuyo pa zaka 4 za zimenezi, misozi inaumanso. Panali malo opanga misozi m’maso mwanga, koma sanali kugwira ntchito.
Patapita zaka 5, sindinathenso kulira ngakhale ndidayesa bwanji. Patapita zaka zingapo za zimenezi, ndinanyansidwa ndekha ndi kubwereranso m’Baibulo.
 
 

Lamulo Ndi Lodziwitsa Uchimo

 
Kodi ife tiyenera kuzindikira chiyani za Lamulo?
Sitingasunge konse Lamulo.
 
Mu Aroma 3:20, ife timawerenga kuti “Pakuti uchimo udziwika ndi lamulo.” Ndinatenga izi ngati uthenga waumwini kwa mtumwi Paulo ndipo ndinakhulupirira kokha mau amene ndinasankha. Koma pamene misozi yanga idauma sindidathe kupitiriza moyo wanga wa chikhulupiriro.
Choncho, ndinkachimwa mobwereza bwereza ndipo ndinapeza kuti ndidali ndi uchimo mu mtima mwanga komanso kuti zinali zosatheka kukhala motsatila Lamulo. Sindinathe kulinyamula ilo. Koma sindikanatha kutaya Lamulo chifukwa ndinkakhulupirira kuti linaperekedwa kuti limveredwe. Pamapeto pake, ndinakhala wachilamulo monga iwo amene akuoneka m’Malemba. Zinakhala zovuta kwambiri kupitiriza moyo wachikhulupiriro.
Choncho, kuti ndichoke mu zovuta, ndinapemphera ndi kufunafuna Ambuye moona mtima. Kenako, ndinakumana ndi Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu Woyera kudzera m’Mau, ndi kudziwa komanso kukhulupilira kuti machimo anga onse adaomboledwa(Kuchotsa Uchimo).
Nthawi zonse pamene ndinkaona mau akuti ndinalibe uchimo, zinali monga mphepo ya yaziyazi yowomba mu mtima mwanga. Ndidali ndi uchimo wambiri kuti powerenga Lamulo, ndinayamba kuzindikira machimo amenewo. Ndidaphwanya Malamulo onse Khumi mu mtima mwanga. Kuchimwa mu mtima ndi uchimonso, ndipo mosadziwa ndinakhala wokhulupilira mu Lamulo.
Pamene ndinkasunga Lamulo ndinali wosangalala. Koma pamene sindinkasunga Lamulo, wachisoni, wopsa mtima komanso wokwiya. Pamapeto pake, ndinakhala otopa nalo lonse. Ndikanaphunzitsidwa kokha kuchokera pachiyambi kuti, “Ayi, ayi. Pali tanthauzo lina ku Lamulo. Ilo limakuonetsa iwe kuti ndiwe mulu wa uchimo; iwe umakonda ndalama, umakonda amuna kapena akazi, komanso umakonda zinthu zimene ndi zokongola kudziyang’ana. Iwe uli ndi zinthu zimene umakonda kwambiri kuposa God. Iwe ukufuna kutsata zinthu za dziko lapansi. Lamulo laperekedwa kwa iwe, osati kuti usunge, koma kuti udzizindikire wekha monga wochimwa wokhala ndi zoipa mu mtima mwako.”
Ngati winawake akanandiphunzitsa kokha m’mbuyomu, sindikadavutika kwa zaka 10. Motero ndidakhala pansi pa Lamulo kwa zaka 10 kufikira pamene ndinazindikira zimenezi. 
Lamulo lachinayi ndilakuti “Udzikumbukira tsiku la Sabata, likhale lopatulika.” Ilo limatanthauza kuti ife sitiyenera kugwira ntchito pa tsiku la Lamlungu. Zikutanthauza kuti ife tiyenera kuyenda, osati kukwera galimoto ngati ife tikupita maulendo atali atali. Ndipo ndinkaganiza kuti ndiyenera kuyenda kupita kumalo kumene ndimakalalikira kuti ndikhale wolemekezeka. Pomaliza zonse, ndinali pafupi kulalikira Chilamulo. Choncho ndinaganiza ndinkayenera kuchita zimene ndinalalikira. Zinali zovuta kwambiri kuti ndinkafuna kusiya.
Monga kwalembedwa apa kuti, “Uwerenga bwanji?” sindinamvetsetse funso limeneli ndipo ndinavutika kwa zaka 10. Wachilamuloyo nayenso anamvetsetsa molakwika ilo. Iye ankaganiza kuti ngati iye angalemekeze Lamulo ndi kukhala mosamala, iye adzadalitsdwa pamaso pa God.
Koma Yesu anamuuza iye kuti, “Uwerenga bwanji?” Inde, walondola; iwe ukulitenga ilo monga lalembedwera. Yesa ndi kusunga ilo. Iwe udzakhala ndi moyo ngati uchita icho, koma udzafa ngati sudzachita. Mphotho yake ya uchimo ndi imfa. “Iwe udzafa ngati sudzachita.” (Chotsutsa cha moyo ndi imfa, sichoncho?)
Koma wachilamuloyu sanamvetsetsebe. Wachilamulo ameneyu ndi ife, inu ndi ine. Ndinaphunzira zaumulungu kwa zaka 10. Ndinayesa chilichonse, kuwerenga chilichonse komanso kuchita chilichonse: kusala kudya, kuona masomphenya, kulankhula m’malilime... ndinawerenga Baibulo kwa zaka 10 ndi kuyembekeza kukwaniritsa china chake. Koma muuzimu ndinali munthu wa khungu.
N’chifukwa chake wochimwa ayenera kukumana ndi munthu amene angamuthandize kuona kuti Mpulumutsi ndiye Ambuye wathu Yesu. Kenako akuzindikira kuti “Aha! Sitingathe konse kusunga Lamulo. Ngakhale titayesetsa kwambiri bwanji, timangopita ku gahena poyesera. Koma Yesu anabwera kudzatipulumutsa ndi madzi ndi Mzimu Woyera Woyera! Aleluya!” Tikhoza kuomboledwa ndi madzi ndi Mzimu Woyera. Ndi chisomo, mphatso ya God. Choncho ife tikuyamika Ambuye.
Ndinali wamwayi kuchoka mu njira yosowa chiyembekezo, koma ena amatha moyo wawo wonse kuphunzira zaumulungu mopanda phindu ndipo sadziwa choonadi mpaka tsiku lakufa kwawo. Ena amakhulupirira kwa zaka zambiri kapena kuchokera ku m’badwo mpaka m’badwo koma sabadwanso mwatsopano konse.
Timachotsedwa kukhala ochimwa pamene tizindikira kuti sitingathe konse kusunga Lamulo, kenako timaima pamaso pa Yesu ndi kumvera uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu Woyera. Tikakumana ndi Yesu, timamaliza maweruzo onse ndi matemberero onse. Ndife ochimwa kwambiri, koma timakhala olungama chifukwa Iye anatipulumutsa ndi madzi ndi mwazi.
Yesu anatiuza ife kuti sitingathe konse kukhala mwa chifuniro Wake. Iye ananena zimenezi kwa wachilamuloyu, koma iye sanamvetsetse. Choncho Yesu anamuuza iye nkhani kuti amuthandize iye kumvetsetsa.
 
Kodi ndi chiyani chimapangitsa anthu kugwa mmoyo wa chikhulupiriro?
Uchimo
 
“Munthu wina anatsika kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Yeriko; ndipo anagwa m’manja a achifwamba amene anamvula zovala, namkwapula, nachoka atamsiya wofuna kufa.” (Luka 10:30) Yesu ankamuuza iye kuti aliyense wavutika moyo wake wonse monga munthu ameneyu anamenyedwa ndi achifwamba ndi kutsala pang’ono kufa.
Munthu wina anatsika kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Yeriko. Yeriko ndi dziko lapadziko ndipo Yerusalemu imaimira mzinda wa chipembedzo mzinda wa chikhulupiriro, wa odzitamandira a lamulo. Ikutiuza ife kuti ngati ife tidzakhulupilira mwa Kristu monga chipembedzo chathu, ife sitingakwanitse koma kuonongeka.
“Munthu wina anatsika kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Yeriko; ndipo anagwa m’manja a achifwamba amene anamvula zovala, namkwapula, nachoka atamsiya wofuna kufa.” Yerusalemu unali mzinda waukulu wokhala ndi chiwerengero chachikuru cha anthu. Kunali mkulu wansembe, khamu la ansembe, Alevia ndi anthu ambiri odziwika bwino achipembedzo kumeneko. Kunali ambiri amene ankadziwa Lamulo bwino. Kumeneko, iwo anayesa kukhala motsatila Lamulo, koma analephera pamapeto pake ndi kulunjika ku Yeriko. Iwo ankagwa m’dziko (Yeriko) ndi kukumana ndi achifwamba.
Munthu anagwa m’manja mwa achifwamba panjira yochokera ku Yerusalemu kunka ku Yeriko ndipo anamvula zovala zake. ‘Kumuvula zovala’ kukutanthauza kuti iye anataya chilungamo chake. Ndizosatheka kwa ife kukhala motsatira Lamulo. Mtumwi Paulo ananena mu Aroma 7:19-20 kuti, “Pakuti chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choipa chimene sindichifuna, chimenecho ndichichita. Koma ngati ndichita chimene sindichifuna, si ndinenso amene ndichichita, koma uchimo wakukhalabe m’kati mwanga ndiwo.”
Ndikanakonda ndikanachita zabwino ndi kukhala m’Mau Wake. Koma mu “m’kati mwake mwa mitima ya anthu, mutuluka maganizo oipa, zachiwerewere, zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa.” (Marko 7:21-22)
Chifukwa chakuti izo zili m’mitima mwathu ndi kupitiriza kuturuka, ife timachita zimene sitiyenera kuchita ndipo sitichita zimene ife tiyenera kuchita. Timangobwereza zoipazo m’mitima mwathu. Chimene mdierekezi ayenera kuchita ndi kungotipatsa ife chikoka chaching’ono chochimwira.
 
 
Machimo mkati mwa Mtima wa Mtundu Wonse wa Anthu
 
Kodi ife tingakhale motsatira Lamulo?
Ayi
 
Kwanenedwa mu Marko 7 kuti, “Palibe chimene chimalowa kuchokera kunja chimene chingamudetse iye; koma zinthu zoturuka mwa iye, izo ndi zinthu zimene zimadetsa munthu.”
Yesu akutiuza ife kuti muli maganizo oipa, zaciwerewere, zakuba, zakupha, zacigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, ndi kupusa mu mtima mwa munthu. Ife tonse tili ndi kupha mmitima yathu.
Kulibe amene samapha. Azimai amakalipilira ana awo kuti, “Ayi. Osachita zimenezo. Ndinakuuza iwe kuti usachite zimenezo, otembeleredwa iwe. Ndinati osachita zimenezo.” Ndiyeno, “Inu bwerani kuno. Ine ndinakuuzani inu ndipo ndinakuuzani inu kuti musachite izo. Ndikupha chifukwa cha izi.” Kumeneko ndi kupha. Inu mungaphe ana anu ndi mau anu osaganizira.
Koma ngati tingatulutse mkwiyo wathu pa iwo, ana adzafa. Ife tinapha kale iwo pamaso pa God. Nthawi zina ife timazipseza tokha. “Oh God wanga! Kodi ndi chifukwa chiyani ndachita icho?” Ife timayangana mabala tikamenya ana athu ndi kuganiza kuti ife tiyenera kukhala osokonezeka kuchita zimemezo. Ife timachita choncho chifukwa chakuti tili ndi kupha m’mitima mwathu.  
Choncho ‘Ndimachita zimene sindifuna kuchita’ zikutanthauza kuti ife timachita zoipa chifukwa chakuti ndife oipa. Ndipo ndi zophweka kwambiri kwa Satana kutiyesa ife kuti tichimwe.
Tiyeni tinene kuti munthu wina amene sanaomboledwe wakhala mu kachisi kwa zaka 10, kuyangana ku khoma ndi kulingalira ngati Sung-chol, wansembe wotchuka wa Chibuddha wa Chikorea. Ndizabwino pamene wakhala poyang’ana nkhope yake ku khoma, koma wina wake ayenera kubweretsa chakudya ndi kuchotsa zonyansa.
Kenako iye ayenera kuyang’anizana ndi winawake. Sizingakhale vuto ngati anali mwamuna, koma tiyerekeze kuti anali mkazi wokongola. Ngati angamuone iye mwamwai, kukhala kwake konse kudzakhala kopanda nchito. Amaganiza, “Sindiyenera kuchita chigololo; ndili nacho mu mtima mwanga, koma ndiyenera kuchichotsa. Ndiyenera kuchigwedeza. Ayi! Choka mu maganizo anga!”
Koma khama lake limatha pa nthawi pamene iye wamuona. Nkaziyo akanyamuka, iye amayang’ana mu mtima mwake. Zaka 10 zogwira ntchito molimbika, zonse pachabe.
Ndizophweka kwambiri kwa Satana kuchotsa chilungamo cha munthu. Zonse zimene Satana ayenera kuchita ndi kukankha machimo awo pang’ono. Pamene anthu akuvutika kuomboledwa, iwo amapitiriza kugwa mu uchimo. Anthu otero amapereka chachikhumi mokhulupirika Lamlungu lililonse, kusala kudya kwa masiku 40, masiku 100 a mapemphero am’mawa... koma Satana amawayesa iwo ndi zinthu zabwino m’moyo.
“Ndikadakonda ndikanakupatsa iwe udindo wofunika mu kampani, koma ndiwe m’Kristu ndipo iwe sungagwire ntchito Lamlungu, kodi iwe ungagwire? Ndi udindo wapamwamba ndithu. Mwina iwe ungamagwire ntchito kwa ma Lamlungu atatu ndi kupita ku mpingo pa mwezi kamodzi. Kenako iwe ungamasangalale ndi kutchuka kwapamwamba ndi kukhala ndi malipiro aakulu. Ukuona bwanji?” Pa zimenezi, kwenikweni anthu 100 pa 100 adzagulidwa. 
Ngati zimenezi sizinagwire ntchito pali iwo amene ali ofooka kwa akazi. Satana amaika mkazi patsogolo pake, ndipo amagwa naye m’chikondi pomwepo ndi kuiwala God mosachedwa. Umo ndi momwe chilungamo cha munthu chimavulidwira.
Ngati ife tiyesa kukhala mwa Lamulo, zonse zomwe timakhala nazo pamapeto pake ndi mabala a uchimo, kupweteka komanso umphawi; ife timataya chilungamo chathu. “Munthu wina anatsika kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Yeriko; ndipo anagwa m’manja a achifwamba amene anamvula zovala, namkwapula, nachoka atamsiya wofuna kufa.”
Zimenezi zikutanthauza kuti ngakhale ife tingayese kukhala mu Yerusalemu pokhala motsatila chifuniro cha God Woyera, ife tidzapunthwa nthawi ndi nthawi chifukwa cha zofooka zathu ndipo ife tidzaonongeka.
Ndipo kenako ife tidzapemphera molapa pamaso pa God. “Ambuye, ndachimwa. Chonde ndikhululukireni; sindidzachitanso. Ndikukulonjezani kuti zimenezi kwenikweni zikhala zotsiriza. Ndikupempha ndikukupemphani kuti mundikhululukire kamodzi kokha.”
Koma izo sizimakhala nthawi yaitali konse. Anthu sangakhale m’dziko lino osachimwa. Akhoza kuzipewa kangapo, koma sizingatheke kuti asachimwenso. Choncho machimo amachitidwanso. “Ambuye, chonde ndikhululukireni.” Ngati izi zipitirira, iwo achoka ku mpingo (chipembedzo). Iwo amatengeka kuchoka kwa God chifukwa cha machimo awo ndipo adzakathera ku gahena.
Kupita ku Yeriko kukutanthauza kugwa m’dziko ladziko, kuyandikira ku dziko ndi kutalikirana ndi Yerusalemu. Pachiyambi, Yerusalemu amakhalabe pafupi kwambiri. Koma pamene kuzungulira kwa kuchimwa ndi kulapa kukubwerezedwa, ife timadzipeza tokha titaima m’misewu ya Yeriko, titagwa mwakuya m’dziko lapansi.
 
Kodi ndani angapulumutsidwe?
Iwo amene amasiya kuyesa pa iwo okha
 
Kodi munthu anakumana ndi ndani panjira popita ku Yeriko? Iye anakumana ndi achifwamba. Munthu amene samakhala ngakhale mwa Lamulo amakhala galu wonyozeka. Iye amamwa, ndi kugona paliponse, kukodza paliponse. Galu ameneyu amadzuka tsiku lotsatira ndi kumwanso. Galu wonyozeka amadya zinyansi zake. Icho ndi chifukwa chake iye ndi galu. Iye amadziwa kuti sayenera kumwa. Iye amalapa m’mawa wotsatira koma amamwanso.
Zili monga munthu amene anakumana ndi achifwamba pa njira yopita ku Yeriko. Iye wasiyidwa m’mbuyo, kufulazidwa ndi kutsala pang’ono kufa. Muli uchimo okha mu mtima mwake. Izi ndi zomwe munthu ali.
Anthu amakhulupirira mwa Yesu ndi kukhala molingana ndi Lamulo mu Yerusalemu koma asiyidwa ndi tchimo lokha mu mitima yawo. Zonse zomwe iwo akuyenera kuwonetsa ku moyo wao wachipembedzo ndi mabala a uchimo. Iwo amene ali ndi uchimo m’mitima mwao amaponyedwa mu gahena. Iwo amadziwa izo koma sadziwa zochita. Kodi inu ndi ine sitinakhalepo kumeneko? Inde. Tonse tinali chimodzimodzi.
Wachilamulo amene sanamvetsetse Lamulo la God akanavutika moyo wake wonse koma potsiriza akathere ku gehena, atavulazidwa. Iye ndife, inu ndi ine.
Yesu yekha angatipulumutse ife. Pali anthu ambiri anzeru otizungulira ndipo amadzionetsera nthawi zonse ndi zimene amadziwa. Onse amadzipangitsa ngati amakhala moyo mogwirizana ndi Lamulo la God. Sangakhale oona mtima kwa iwo eni. Sanganene molunjika chimene chiri chabwino kapena cholakwika, koma nthawi zonse amalimbikira kukonzekeretsa maonekedwe awo akunja kuti awonekere okhulupirika.
Pakati pa iwo pali ochimwa opita ku Yeriko, iwo amene amenyedwa ndi achifwamba komanso amene afa kale. Ife tiyenera kudziwa momwe tilili ofooka pamaso pa God.
Ife tiyenera kuvomereza pamaso Pake kuti, “Ambuye, ndidzapita kugahena ngati Inu simudzandipulumutsa. Chonde ndipulumutseni. Ndidzapita kulikonse kumene Inu mukufuna kaya kukugwa mvula ya matalala kapena mikuntho, ngati Inu mundilola kumva uthenga wabwino oona. Ngati Inu mundisiya ine, ndidzapita ku gahena. Ndikukudandaulirani Inu kuti mundipulumutse.”
Iwo amene amadziwa kuti akulunjika ku gahena, iwo amene amasiya kuyesa pa iwo okha ndi kugwiritsitsa kwa ambuye, amenewa ndi amene angapulumutsidwe. Sitingathe konse kupulumutsidwa patokha.
Ife tiyenera kudziwa kuti tili monga munthu amene anagwa m’manja a achifwamba.
 
Ulaliki uwu ukupezekanso mu mtundu wa ebook. Dinani pachikuto cha buku pansipa.
KODI MWABADWADI MWATSOPANO MWA MADZI NDI MZIMU WOYERA? [Kusindikiza Kokonzedwanso Kwatsopano]