(Mateyu 3:13-17)
“Pamenepo Yesu anachokera ku Galileya nadza ku Yordani kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye. Koma Yohane anati amkanize, nanena, Ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi? Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero. Pamenepo anamlola Iye. Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anatuluka m’madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu(God) wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye; ndipo onani, mau akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.”
Kodi Pali Winawake Amene Akuvutikabe ndi Uchimo?
| Kodi ukapolo wathu ku uchimo unatha? |
| Inde. |
Ambuye God wathu wadula unyolo wonse wa uchimo kwa anthu onse. Iwo onse amene akuvutika pansi pa uchimo ndi akapolo. Iye anachotsa machimo athu onse. Kodi pali winawake amene akuvutikabe ndi uchimo?
Ife tiyenera kumvetsetsa kuti nkhondo yathu ndi uchimo yatha. Ife sitidzavutikanso ndi uchimo. Ukapolo wathu ku uchimo unatha pamene Yesu anatiombola ife; machimo onse anatheratu pamenepo. Machimo athu onse athetsedwa ndi Mwana Wake. God analipira machimo athu onse kudzera mwa Yesu, amene anatimasula ife, kwamuyaya.
Kodi inu mukudziwa momwe anthu avutikira ndi machimo ao? Zinayamba kuchokera mu nthawi ya Adamu ndi Heva. Mtundu wa anthu umavutika ndi uchimo otengera kwa Adamu.
Koma God wathu anapanga pangano lomwe lalembedwa mu Genesis 3:15, ndipo panganolo linali lakuti Iye adzaombola ochimwa onse. Iye ananena kuti anthu adzaomboledwa ku machimo ao kudzera mu nsembe ya Yesu Kristu kudzera mwa madzi ndi Mzimu Woyera. Ndipo pamene nthawi inafika, Iye anatuma Mpulumutsi wathu, Yesu, kudzakhala pakati pathu.
Iye analonjezanso kutuma Yohane Mbatizi patsogolo pa Yesu ndipo Iye anasunga lonjezo Lake.
Mu Marko 1:1-8, “Chiyambi chake cha Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu(God). Monga mwalembedwa mu Yesaya mneneri, Ona, ndituma mthenga wanga patsogolo pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu. Mau a wofuula m’chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake. Yohane anadza nabatiza m’chipululu, nalalikira Ubatizo wa kutembenuka mtima wakuloza ku chikhululukiro (kuchotsa machimo) cha machimo. Ndipo anatuluka a ku dziko lonse la Yudeya, ndi a ku Yerusalemu onse, nadza kwa iye nabatizidwa ndi iye mumtsinje Yordani, powulula machimo ao. Ndipo Yohane anavala ubweya wa ngamira, ndi lamba lachikopa m’chuuno mwake, nadya dzombe ndi uchi wakuthengo. Ndipo analalikira, kuti, Wondipambana ine mphamvu akudza pambuyo panga, sindiyenera kuwerama kumasula zingwe za nsapato zake. Ndakubatizani inu ndi madzi; koma Iye adzakubatizani ndi Mzimu Woyera.”
Yohane Mbatizi, Mboni komanso Wotsogolera wa Uthenga Wabwino
| Kodi Yohane Mbatizi ndi ndani? |
| Mkulu wansembe wotsiriza komanso woimirira wa mtundu wonse wa anthu |
Iwo amene amakhulupilira mwa Yesu abatizidwa. Ubatizo umatanthauza; ‘Kutsukidwa, Kukwiriridwa, Kumizidwa, Kupereka.’ Pamene Yesu anabatizidwa, chilungamo cha God chinakwaniritsidwa. ‘Chilungamo’ ndi ‘Δικαιοσύνη (Dikaiosynē)’ mu Chigiriki omwe amatanthauza ‘Kukhala olungama,’ ndipo amatanthauzanso ‘Choyenera kwambiri,’ ‘Chogwirizana kwambiri.’
Kuti Yesu abatizidwe kunali kwa Iye kuti akhale Mpulumutsi m’njira yoyenera kwambiri komanso yabwino. Choncho, iwo amene amakhulupilira mwa Yesu amalandira mphatso ya chiombolo kuchokera kwa God pokhulupilira mu madzi a Ubatizo Wake, Mtanda ndi Mzimu Woyera.
Mu Chipangano Chatsopano, Yohane Mbatizi ndi mkulu wansembe wotsiriza wa Chipangano Chakale. Tiyeni tione Mateyu 11:10-11. “Uyu ndiye amene kunalembedwa za iye, kuti, Onani Ine nditumiza mthenga wanga pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu m’tsogolo mwanu. Indetu ndinena kwa inu, Sanauke wakubadwa mwa mkazi munthu wamkulu woposa Yohane Mbatizi; koma iye amene ali wochepa mu Ufumu wa Kumwamba amkulira iye.”
Malemba amanena kuti Yohane Mbatizi ndi woimirira wa mtundu wa anthu. Ndipo monga mkulu wansembe mu nthawi ya Chipangano Chatsopano, iye anasamutsira machimo onse a dziko lapansi pa Yesu, motero kutumikira ntchito ya mkulu wansembe wa Chipangano Chakale.
Yesu mosabisa adachitira umboni za Yohane. Iye ananena, mu Mateyu 11:13-14 kuti, “Pakuti aneneri onse ndi cilamulo cinanenera kufikira pa Yohane. Ndipo ngati mufuna kulandira, uyu ndiye Eliya amene amati akudza.” Choncho, Yohane Mbatizi, amene anabatiza Yesu, anali mbadwa ya mkulu wansembe Aroni komanso mkulu wansembe wotsiriza. Baibulo limachitiranso umboni za Yohane kukhala mbadwa ya Aroni m’Chipangano Chakale (Luka 1:5, 1 Mbiri 24:10).
Nanga kodi ndi chifukwa chiyani Yohane ankakhala m’chipululu yekha, kuvala zovala zopangidwa ndi ubweya wa ngamila? Kutenga udindo wa mkulu wansembe. Komanso monga woimirira wa mtundu wa anthu, Yohane Mbatizi sakanakhala pakati pa anthu. Choncho iye anafuula kwa anthu kuti “Lapani, ana a njoka inu!” ndi kubatiza iwo ku chipatso cha kulapa, zimene zinabweza anthu kwa Yesu, amene adzachotsa machimo ao onse. Yohane Mbatizi anapatsira machimo a dziko lapansi pa Yesu kuti tipulumutsidwe.
Mitundu Iwiri ya Ubatizo
| Kodi ndi chifukwa chiyani Yohane Mbatizi ankabatiza anthu? |
| Kutsogolera anthu kuti alape ku machimo ao onse ndi kukhulupilira mu Ubatizo wa Yesu kuti apulumutsidwe |
Yohane Mbatizi anabatiza anthu ndipo kenako anabatiza Yesu. Woyamba unali ‘Ubatizo wa kulapa’ umene unkaitana ochimwa kuti abwelere kwa God. Anthu ambiri amene anamva mau a God kudzera mwa Yohane anasiya mafano ao ndi kubwelera kwa God.
Ubatizo wa chiwiri unali Ubatizo wa Yesu, Ubatizo umene unapatsira machimo onse a dziko lapansi pa Yesu. Yohane Mbatizi anabatiza Yesu kuti akwaniritse chilungamo cha God. Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi kuti apulumutse anthu onse ku machimo ao (Mateyu 3:15).
Kodi ndi chifukwa chiyani Yohane anayenera kubatiza Yesu? Kuti afafanize machimo a dziko lapansi, God adalola Yohane kupereka uchimo onse pa Yesu kuti anthu amene anakhulupilira mwa Yesu apulumutsidwe.
Yohane Mbatizi anali mtumiki wa God amene ntchito yake inali kuthandiza mtundu wonse wa anthu kuti utsukidwe ku machimo ao ndipo iye anali woimirira wa mtundu wa anthu amene anachitira umboni ku Uthenga Wabwino wa chiombolo. Choncho, Yohane adayenera kukhala yekha m’chipululu. Mu nthawi ya Yohane Mbatizi, anthu a Israyeli anali onse owonongeka komanso owola motheratu.
Choncho God adanena m’Chipangano Chakale, Malaki 4:5-6 kuti, “Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova. Ndipo adzabwezera mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate ao; (kuopa kuti ndingadze ndi kukantha dziko ndi temberero.—NKJV)”
Mmaso mwa God, anthu onse a Israyeli amene ankapembedza Yehova anali owonongeka. Palibe amene anali wolungama pamaso Pake. Atsogoleri achipembedzo a kachisi, mwa chitsanzo, ansembe, achilamulo ndi alembi anali makamaka owola motheratu kwenikweni mpaka pachimake. Israyeli ndi ansembe sankapereka nsembe malingana ndi Lamulo la God.
Ansembe adasiya kuika kwa manja komanso mwambo wopereka mwazi, zimene God adawaphunzitsa iwo ku chitetezero cha machimo ao. Kwalembedwa kuti ansembe m’masiku a Malaki adasiya kupereka nsembe, kuika kwa manja, komanso kupereka kwa mwazi m’mwambo.
Choncho, Yohane Mbatizi sakanakhala ndi iwo. Choncho Yohane Mbatizi anapita m’chipululu ndi kufuula. Kodi iye ananena chiyani?
Kwalembedwa mu Marko 1:2-3, m’mau a mneneri Yesaya kuti, “Monga mwalembedwa mu Yesaya mneneri, Ona, ndituma mthenga wanga patsogolo pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu. Mau a wofuula m’chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake.”
Mau m’chipululu anafuula kwa anthu kuti alandire Ubatizo wa kulapa. Kodi ‘Ubatizo wa kulapa’ umene Baibulo limalankhula ndi chiyani? Ndi Ubatizo umene Yohane Mbatizi anafuulira; Ubatizo woitanira anthu kubwerera kwa Yesu kuti iwo akhulupirire mwa Yesu amene adzachotsa machimo ao onse ndi kupulumutsidwa. Ubatizo wa kulapa unali kuti uwatsogolere iwo ku chipulumutso.
“Lapani ndi kubatizidwa, ndipo Yesu adzabatizidwa m’njira yomweyo kuti achotse machimo anu onse.” Kufuula kwa Yohane Mbatizi kunali kwakuti Yesu adzachotsa machimo onse a dziko lapansi ndi kuweruzidwa pa Mtanda kuti apulumutse anthu onse kuti iwo abwerere kwa God.
“Ndakubatizani inu ndi madzi; koma iye adzakubatizani ndi Mzimu Woyera” (Marko 1:8). ‘Adzakubatizani ndi Mzimu Woyera’ akutanthauza kutsuka machimo anu onse. Kubatiza kumatanthauza ‘Kutsuka.’ Ubatizo wa Yesu pa Yordano umatiuza ife kuti Mwana wa God motero anabatizidwa ndi kuchotsa machimo athu onse kuti atipulumutse ife.
Choncho, ife tiyenera kuchoka ku uchimo ndi kukhulupilira mwa Iye. Iye ndi Mwanawankhosa amene achotsa machimo a anthu onse. Ndipo uwu ndi Uthenga Wabwino wa chiombolo umene Yohane Mbatizi anachitira umboni.
Ntchito ya Mkulu Wansembe ya Chitetezero cha Machimo
| Kodi ndi ndani anakonza njira ya chipulumutso? |
| Yohane Mbatizi |
Mneneri Yesaya adanenera kuti, “Munene inu zotonthoza mtima kwa Yerusalemu, nimufuulire kwa iye, kuti nkhondo yake yatha, kuti kuipa (mphulupulu) kwake kwakhululukidwa; kuti iye walandira mowirikiza m’dzanja la Yehova, chifukwa cha machimo ake onse” (Yesaya 40:2).
Yesu Kristu anachotsa machimo a inu ndi ine komanso a aliyense mosachotsera; uchimo woyambilira, machimo atsopano, komanso ngakhale machimo amtsogolo anatsukidwa kudzera mu Ubatizo Wake. Iye anatiombola ife tonse. Ife tonse tiyenera kudziwa za chiombolo.
Kuti tipulumutsidwe ku machimo athu onse, ife tiyenera kukhulupilira mu Uthenga Wabwino umene umanena kuti Yohane Mbatizi anasamutsira machimo onse pa Yesu kudzera m’njira ya Ubatizo.
Ndi kusamvetsetsa kuganiza kuti “chifukwa chakuti God ndi chikondi, ife tingalowe ku ufumu wa kumwamba pokhulupilira kokha mwa Yesu, ngakhale ife tili ndi uchimo mu mtima mwathu.”
Kuti tiomboledwe ku machimo athu onse, ife tiyenera kukhulupilira mu Ubatizo Wake, umene Yohane Mbatizi anapatsira machimo onse a dziko lapansi pa Yesu. Ndi kudzera ‘m’madzi’ kuti Yohane Mbatizi anapatsira machimo onse a mtundu wa anthu pa Yesu.
Chinthu choyamba chimene God anachita kuti atipulumutse ife chinali kutuma Yohane Mbatizi ku dziko lino lapansi. Mthenga wa God, Yohane Mbatizi anatumizidwa monga kazembe wa Mfumu, amene anasamutsira machimo onse a dziko lapansi kwa Yesu kudzera mu Ubatizo. Iye anatumikira ntchito ya mkulu wansembe ku mtundu wonse wa anthu.
God anatiuza ife Iye anatuma mthenga Wake, Yohane Mbatizi, kwa ife. “Ndituma mthenga wanga patsogolo pa nkhope yanu.” Pa nkhope Yanu akutanthauza patsogolo pa Yesu. Kodi chinali chifukwa chiyani Iye anatumira Yohane patsogolo pa Yesu? Kunali kuti apereke machimo onse a dziko lapansi kwa Yesu, Mwana wa God, kudzera mu Ubatizo. “Amene adzakonza njira Yanu.” Izi ndi zomwe Iye ankatanthauza.
Kodi ndi ndani amene anakonza njira kuti tiomboledwe ndi kupita kumwamba? Yohane Mbatizi. ‘Yanu’ akutanthauza Yesu ndipo ‘Wanga’ akutanthauza God Mwini. Choncho, pamene Iye ananena kuti, “Ndituma mthenga wanga patsogolo pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu.” kodi chikutanthauza chiyani?
Kodi ndi ndani adzakonza njira yathu kuti ife tipite kumwamba? Yohane Mbatizi anasamutsira machimo athu onse pa Yesu ndi cholinga chakuti ife tikhulupirire kuti Yesu anatitsukira machimo athu onse; ntchito yake inali kupereka machimo pobatiza Yesu Kristu. Anali Yesu ndi Yohane amene anapanga kukhala chotheka kwa ife kukhulupilira mu choonadi ndi kuomboledwa.
Kodi chipulumutso chathu chimatengera pa chiyani? Icho chimatengera ngati ife timakhulupirira mu ntchito za Yesu, Mwana wa God, komanso choona chakuti mthenga wa God adapereka machimo onse a dziko lapansi pa Iye. Ife tonse tiyenera kudziwa Uthenga Wabwino wa machimo otichotidzera. God Atate anatuma mthenga Wake patsogolo, m’modzi amene adzabatiza Mwana Wake, ndi kumupanga iye kukhala woimirira wa mtundu wa anthu. Motero, Iye anatsiriza ntchito ya chiombolo kwa ife.
God anatuma mtumiki Wake Yohane Mbatizi kuti abatize Mwana Wake, ndi cholinga chakuti Yohane Mbatizi akonze njira ya chipulumutso kwa iwo amene akhulupilira mwa Mwana Wake. Icho ndiye chifukwa cha Ubatizo wa Yesu. Ubatizo umene Yesu analandira kwa Yohane Mbatizi unali chiombolo kudzera momwe machimo onse a mtundu wa anthu anaperekedwa pa Yesu kuti anthu onse akhulupilire mwa Yesu ndi kupita kumwamba.
Ngakhale machimo amtsogolo a mtundu wa anthu anaperekedwa pa Yesu kudzera mu Ubatizo Wake. Yesu ndi Yohane Mbatizi pamodzi anakonza njira yopitira ife kumwamba. Mwa njira imeneyi, God anavumbulutsa chinsinsi cha chiombolo kudzera mwa Yohane Mbatizi.
Monga woimirira wa aliyense wa ife, Yohane Mbatizi anabatiza Yesu ndi cholinga chakuti ife tikhulupirire mu chiombolo chathu ndi kupita kumwamba. Iye anasamutsira uchimo onse kwa Yesu kudzera mu Ubatizo. Iyi ndi nkhani yosangalatsa ya chiombolo, Uthenga Wabwino.
Kodi ndi Chifukwa Chiyani Yohane Mbatizi Anabadwa?
| Kodi ife tingakhulupirire mwa Yesu kudzera mwa ndani? |
| Yohane Mbatizi |
Mu Malaki 3:1, kwalembedwa kuti, “Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga.” Inu muyenera kuwerenga Baibulo mosamala. Kodi ndi chifukwa chiyani God anatuma mthenga Wake patsogolo pa Yesu? Kodi ndi chifukwa chiyani Yohane Mbatizi anabadwa miyezi 6 Yesu asanabadwe?
Ife tiyenera kumvetsetsa zimene Baibulo limanena. Muli gawo m’Chipangano Chakale pa utumiki wa mkulu wansembe Aroni. Aroni anali mkulu wake wa Mose. Iye ndi ana ake anadzodzedwa monga ansembe ndi God. Alevi ena ankagwira ntchito pansi pa iwo, kuwabweretsera iwo ziwiya zosiyanasiyana, kusakaniza ufa wa mkate ndi zotero, pamene ana a Aroni ankapereka nsembe mkati mwa Chihema choyera.
Choncho ana a Aroni anadzozedwa kugawana ntchito yofanana pakati pao, koma pa Tsiku la Chitetezero, tsiku la khumi la mwezi wa chisanu ndi chiwiri, mkulu wansembe yekha ankaperekera nsembe ya chitetezero anthu ake.
Mu Luka 1:5, muli nkhani ya m’badwo wa Yohane Mbatizi. Ife tiyenera kumvetsetsa molondola za mthenga wa God ameneyu kuti timvetsetse Yesu molondola. Ife timakonda kuganiza kwambiri za Yesu, koma kunyalanyaza kwambiri za Yohane Mbatizi, amene anadza Iye asanabwere. Ndikufuna ndikuthandizeni inu kumvetsetsa.
“Chiyambi chake cha Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu(God). Monga mwalembedwa mu Yesaya mneneri, Ona, ndituma mthenga wanga patsogolo pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu.” (Marko 1:1-2) Uthenga Wabwino wa kumwamba nthawi zonse umayamba ndi Yohane Mbatizi.
Pamene ife tamvetsetsa bwino za Yohane Mbatizi, ife tingamvetsetse bwino ndi kukhulupilira mu Uthenga Wabwino wa chiombolo cha Yesu. Ndi chimodzimodzi ndi kumvera kwa akazembe amene tamwaza pa dziko lonse lapansi kuti timvetsetse zochitika za maiko onse. Pamene ife tadziwa za Yohane Mbatizi, ife tingamvetsetse chiombolo cha God bwino bwino.
Kodi ndi zomvetsa chisoni bwanji, komabe, kuti Akristu ambiri masiku ano saona kufunika kwa Yohane. God sanatume Yohane Mbatizi chifukwa chakuti Iye anali wotopetsa ndi analibe chilichonse chochita. Mauthenga Abwino onse anayi a Chipangano Chatsopano amalankhula za Yohane Mbatizi asanalankhule za chiombolo cha Yesu.
Koma alaliki a lero amanyalanyaza iye motheratu ndi kuuza anthu kuti kukhulupilira chabe mwa Yesu ndi kokwanira kupulumutsidwa. Iwo kwenikweni akutsogolera anthu kukhala monga ochimwa miyoyo yao yonse ndi kuthera mu gahena. Ngati inu mumakhulupirira chabe mwa Yesu popanda kumvetsetsa ntchito ya Yohane Mbatizi, Chikristu chimakhala chabe chipembedzo china kwa inu. Kodi inu mungaomboledwe bwanji ku machimo anu ngati inu simudziwa choonadi? Ndi zosatheka.
Uthenga Wabwino wa chiombolo si wapafupi kapena wophweka motero. Anthu ambiri amaganiza kuti chiombolo chimagona mu chikhulupiliro chathu mu Mtanda chifukwa chakuti Yesu anafa pa Mtanda chifukwa cha ife. Koma ngati inu mumakhulupirira kokha mu kupachikidwa popanda kudziwa choonadi cha anasamutsira machimo, palibe chikhulupiriro chimene chidzakutsogolerani ku chiombolo chathuthu.
Choncho, God anatuma Yohane Mbatizi kuti dziko lidziwe momwe chiombolo chidzakwaniritsidwira komanso momwe Yesu adzachotsera machimo a dziko lapansi. Pokhapokha ngati ife tadziwa choonadi ndi pamene ife tidzamvetsetsa kuti Yesu ndi Mwana wa God amene anatengera machimo athu onse kwa Iye Mwini.
Yohane Mbatizi amatiuza ife za choonadi cha chiombolo. Iye amatiuza ife momwe iye anabwerera kudzachitira umboni za uGod wa Yesu, komanso momwe anthu sanamulandilire Iye pamene Kuunika kunatsika ku dziko lino lapansi. Iye anachitiranso umboni mu Yohane 1 kuti anali iye amene anakonza Uthenga Wabwino wa chiombolo pobatiza Yesu Kristu.
Ngati ife tinalibe umboni wa Yohane Mbatizi okhudza chiombolo, kodi ife tikanakhulupirira bwanji mwa Yesu? Ife sitinaonepo Yesu, ndipo pamene ife tachokera ku zikhalidwe zosiyanasiyana komanso zipembedzo, kodi zingatheke bwanji kukhulupirira mwa Yehova?
Pokhala ndi zipembedzo zosiyanasiyana zotero m’dziko lonse lapansi, kodi ife tingadziwe bwanji Yesu Kristu? Kodi ife tingadziwe bwanji kuti Yesu kwenikweni anali Mwana wa God amene anatiombola ife potenga machimo onse a dziko lapansi pa Iye Mwini?
Choncho, ife tiyenera kuyang’ana m’Chipangano Chakale kuti tipeze kuchokera pa chiyambi mau a chiombolo ndi kudziwa kuti Yesu ndi Mpulumutsi wathu. Ife tiyenera kupeza chidziwitso cholondola kuti tikhulupirire molondola. Palibe chimene ife tingachite popanda chidziwitso choona. Kuti tikhulupirire mwa Yesu ndi kupulumutsidwa, ife tiyenera kudziwa Uthenga Wabwino wa chiombolo umene Yohane Mbatizi anachitira umboni komanso ntchito yake mu uwo. Kuti tikhale ndi chikhulupiriro chathunthu mwa Kristu, ife tiyenera kudziwa choonadi cha chiombolo.
Choncho, monga Yesu ananenera kuti, “Ndipo mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani” (Yohane 8:32), ife tiyenera kudziwa choonadi cha chiombolo mwa Yesu.
Zitsimikizo za m’Baibulo
| Kodi mabuku a Uthenga Wabwino anayi amayamba ndi chiyani? |
| Kuyambira pa kubwera kwa Yohane Mbatizi |
Tiyeni tipite patsogolo ndi kuona zitsimikizo zonse za chiombolo m’Baibulo. Tiyeni tivundukule zimene mabuku anayi a Uthenga Wabwino akunena za Yohane Mbatizi, za kuti iye anali ndani, chifukwa chimene iye anatchedwa ‘woimirira wa mtundu wa anthu’ kapena ‘mkulu wansembe wotsiriza,’ momwe machimo onse a dziko lapansi anaperekedwera pa Yesu kudzera mwa iye, komanso ngati Yesu anatengera machimo onse kwa Mwini kapena ai.
Mabuku onse anayi a Uthenga Wabwino amayamba ndi nkhani ya Yohane Mbatizi. Yohane 1:6 amatiuza ife chinthu chofunika kwambiri mu Uthenga Wabwino. Iyo imatiuza ife amene anachita ntchito yopereka machimo onse a dziko lapansi pa Yesu. “Kunali munthu, wotumidwa ndi Mulungu(God), dzina lake ndiye Yohane. Iyeyu anadza mwa umboni kudzachita umboni za kuunikaku, kuti onse akakhulupirire mwa iye” (Yohane 1:6-7).
Iyo ikunena kuti, ‘kuti onse akakhulupirire mwa iye,’ komanso kuti iye anali ‘kudzachita umboni za kuunikaku.’ Kuunika ndi Yesu Kristu. Zikutanthauza kuti Yohane anali wochitira umboni za Yesu kuti onse akakhulupirire mwa iye. Tsopano, tiyeni tiyang’anitsitse pa Mateyu.
Mu Mateyu 3:13-17, “Pamenepo Yesu anachokera ku Galileya nadza ku Yordani kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye. Koma Yohane anati amkanize, nanena, Ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi? Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero. Pamenepo anamlola Iye. Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anatuluka m’madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu(God) wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye; ndipo onani, mau akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.”
| Kodi ndi chifukwa chiyani ife tiyenera kumvetsetsa m’badwo wa Yohane? |
| Chifukwa chakuti Baibulo limatiuza ife kuti Yohane ndi mkulu wansembe wa mtundu wonse wa anthu. |
Yohane Mbatizi anabatiza Yesu. Anali Yohane Mbatizi amene machimo onse a dziko lapansi kwa Yesu Kristu. Mu Luka 1, Luka akulankhula za m’badwo wa Yohane Mbatizi. Tiyeni tione.
Mu Luka 1:1-14, “Popeza ambiri anayesa kulongosola nkhani ya zinthu zinachitika pakati pa ife, monga anazipereka kwa ife iwo amene anakhala mboni ndi atumiki a mau, kuyambira pachiyambi, ndinayesa nkokoma inenso, amene ndinalondalonda mosamalitsa zinthu zonse kuyambira pachiyambi, kulembera kwa iwe tsatanetsatane, Teofilo wabwinotu iwe; kuti udziwitse zoona zake za mau amene unaphunzira. Masiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kunali munthu wansembe, dzina lake Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya; ndi mkazi wake wa ana aakazi a fuko la Aroni, dzina lake Elizabeti. Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu(God), namayendabe m’malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osachimwa. Ndipo analibe mwana, popeza Elizabeti anali wouma, ndipo onse awiri anakalamba. Ndipo panali, pakuchita iye ntchito yakupereka nsembe m’dongosolo la gulu lake, pamaso pa Mulungu(God), monga mwa machitidwe a kupereka nsembe, adamgwera maere akufukiza zonunkhira polowa iye mu Kachisi wa Ambuye. Ndipo khamu lonse la anthu linalikupemphera kunja nthawi ya zonunkhira. Ndipo anamuonekera iye mngelo wa Ambuye, naimirira kudzanja lamanja la guwa la nsembe la zonunkhira. Ndipo Zekariya anadabwa pamene anamuona, ndipo mantha anamgwira. Koma mngelo anati kwa iye, Usaope Zekariya, chifukwa kuti lamveka pemphero lako, ndipo mkazi wako Elizabeti adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane. Ndipo udzakhala nako kukondwera ndi msangalalo; ndipo anthu ambiri adzakondwera pa kubadwa kwake.”
Luka amatiuza ife mwatsatanetsatane za m’badwo wa Yohane. Luka, wophunzira wa Yesu, amafotokoza za m’badwo wa Yohane kuchokera pachiyambi. Luka anaphunzitsa Uthenga Wabwino kwa munthu wotchedwa Teofilo, amene anali wa chikhalidwe china ndipo sanadziwe za Ambuye.
Choncho, kuti amuphunzitse iye za Yesu, Mpulumutsi wa ochimwa, Luka anaganiza kuti iye anafunika kufotokoza za m’badwo wa Yohane Mbatizi mwatsatanetsatane.
Mu Luka 1:5-9, iye akufotokoza kuti, “Masiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kunali munthu wansembe, dzina lake Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya; ndi mkazi wake wa ana aakazi a fuko la Aroni, dzina lake Elizabeti. Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu(God), namayendabe m’malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osachimwa. Ndipo analibe mwana, popeza Elizabeti anali wouma, ndipo onse awiri anakalamba. Ndipo panali, pakuchita iye ntchito yakupereka nsembe m’dongosolo la gulu lake, pamaso pa Mulungu(God), monga mwa machitidwe a kupereka nsembe.”
Apa, chinthu china chinachitika pamene Zakariya ankatumikira God monga mwa machitidwe kupereka. Luka anachitira umboni momveka bwino kuti Zakariya anali mbadwa ya Aroni. Nanga kodi Zakariya anali wa gulu liti? Iyi ndi mfundo yofunika kwambiri.
Iye anafotokoza kuti, “pakuchita iye ntchito yakupereka nsembe pamaso pa Mulungu(God) m’dongosolo la gulu lake, pamaso pa Mulungu(God).” Ife tingaone kuti Luka ankadziwa bwino za Zakariya kuti iye anafotokoza Uthenga Wabwino wa chiombolo kudzera mwa Zakariya ndi Elizabeth.
Pamene ndifenso Amitundu ochokera m’mitundu yosiyanasiyana, ife sitingamvetsetse chipulumutso cha Yesu ngati sichinafotokozedwe mwatsatanetsatane, pang’ono pang’ono. Tiyeni tione tsatanetsatane wake. Yohane Mbatizi anabadwa kwa Zakariya ndi mkazi wake Elisabeti, amene anali m’modzi wa ana akazi a pfuko la Aroni. Tsopano, tiyeni tione pa m’badwo wa Zakariya ndi Yohane.
M’badwo wa Yohane Mbatizi
| Kodi Yohane Mbatizi anali mbadwa ya ndani? |
| Aroni, mkulu wansembe |
Kuti timvetsetse m’badwo wa Yohane Mbatizi, ife tiyenera kuwerenga Chipangano Chakale, 1 Mbiri 24:1-19.
“Ndipo magawidwe a ana a Aroni ndi awa. Ana a Aroni: Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara. Koma Nadabu ndi Abihu anafa, atate wao akali ndi moyo, opanda ana; momwemo Eleazara ndi Itamara anachita ntchito ya nsembe. Ndipo Davide pamodzi ndi Zadoki wa ana a Eleazara, ndi Ahimeleki wa ana a Itamara, anawagawa, monga mwa malongosoledwe ao mu utumiki wao. Ndipo anapeza kuti amuna aakulu a ana a Eleazara anachuluka, a ana a Itamara anachepa; nawagawa motero: pa ana a Eleazara panali khumi mphambu asanu ndi mmodzi, akulu a nyumba za makolo; ndi pa ana a Itamara, monga mwa nyumba za makolo ao, panali asanu ndi atatu. Ndipo anawagawa ndi maere, awa ndi aja; pakuti panali akalonga a malo opatulika, ndi akalonga a kwa Mulungu(God), a ana a Eleazara ndi a ana a Itamara omwe. Ndi Semaya mwana wa Netanele mlembi, ndiye wa Alevi, anawalembera pamaso pa mfumu; ndi akalonga, ndi Zadoki wansembe, ndi Ahimeleki mwana wa Abiyatara, a akulu a nyumba za makolo a ansembe ndi Alevi, anatenga nyumba imodzi ya kholo lake ya Eleazara, ndi imodzi ya Itamara. Ndipo maere oyamba anamgwera Yehoyaribu, wachiwiri Yedaya, wachitatu Harimu, wachinai Seorimu, wachisanu Malikiya, wachisanu ndi chimodzi Miyamini, wachisanu ndi chiwiri Hakozi, wachisanu ndi chitatu Abiya, wachisanu ndi chinai Yesuwa, wakhumi Sekaniya, wakhumi ndi chimodzi Eliyasibu, wakhumi ndi chiwiri Yakimu, wakhumi ndi chitatu Hupa, wakhumi ndi chinai Yesebeabu, wakhumi ndi chisanu Biliga, wakhumi ndi chisanu ndi chimodzi Imeri, wakhumi ndi chisanu ndi chiwiri Heziri, wakhumi ndi chisanu ndi chitatu Hapizeze, wakhumi ndi chisanu ndi chinai Petahiya, wa makumi awiri Yehezikele, wa makumi awiri ndi chimodzi Yakini, wa makumi awiri ndi chiwiri Gamuli, wa makumi awiri ndi chitatu Delaya, wa makumi awiri ndi chinai Maaziya. Awa ndi malongosoledwe ao mu utumiki wao kulowa m’nyumba ya Yehova, monga mwa chiweruzo adawapatsa Aroni atate wao, monga Yehova Mulungu(God) wa Israele anamlamulira.”
Tiyeni tiwerengenso ndime ya 10. “Wachisanu ndi chiwiri Hakozi, wachisanu ndi chitatu Abiya.” Apa, Davide anachita maere kwa aliyense wa ana a Aroni kuti nsembe idziperekedwa mu mndandanda. (Monga nonse mukudziwira, Aroni anali mkulu wake wa Mose. God anadzodza Mose monga womuimira Wake, ndipo Aroni monga mkulu wansembe wa Chihema Choyera pamaso pa Israyeli.)
Alevi ena onse anawasiya pansi pa ulamuliro wa ansembe ndipo Aroni ndi ana ake anatenga ulamuliro pa nsembe zonse pamaso pa God. Davide asanaike dongosolo la kuchita maere, ansembe, mbadwa za Aroni, zinkayenera kuponya maere nthawi zonse ndipo zinkabweretsa chisokonezo chachikuru.
Choncho Davide analongosola moperekera nsembe poika mudongosolo gulu lililonse. Panali magulu 24 mmalongosoledwe ochokera ku zidzukuru za Aroni ndipo wa chisanu ndi chitatu anali Abiya. Ndipo kwanenedwa kuti, “Kunali munthu wansembe, dzina lake Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya.” Choncho Zakariya ndi mkazi wake Elisabeti anali onse mbadwa za Aroni mkulu wansembe.
Anali Zakariya, wansembe wa gulu la Abiya, amene anali atate wa Yohane Mbatizi. Ife tikudziwa kuchokera m’Baibulo kuti iwo ankakonda kukwatirana m’banja limodzi.
Monga inu mukudziwira, Yakobo adakwatira mwana wa amalume ake kumbali ya amayi ake. Ndi kufotokoza kumeneku kwa m’badwo kumene kuli ndi kufunika kwakuya kwambiri. Akuti, “Kunali munthu wansembe, dzina lake Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya.”
Choncho iye anali kwenikweni mbadwa ya Aroni. Ndani? Zakariya, atate wa Yohane Mbatizi. Ichi ndi chinthu chofunika kwambiri pofotokoza chiombolo cha Yesu, ndi utumiki wa Yohane Mbatizi, komanso, kupereka kwa machimo a dziko lapansi pa Yesu.
Ana Okha a Aroni Ayenera Kutumikira monga Ansembe
| Kodi ndi ndani amene amatumikira monga mkulu wansembe mu nthawi ya Chipangano Chakale? |
| Aroni ndi mbadwa zake |
Ndiye kodi ndi pati m’Baibulo pamene pamanena kwenikweni kuti ana a Aroni ayenera kutumikira monga ansembe? Tiyeni tione.
Mu Buku la Numeri 20:22-29, “Ndipo anayenda ulendo kuchokera ku Kadesi; ndi ana a Israele, ndilo khamu lonse, anadza kuphiri la Hori. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni m’phiri la Hori, pa malire a dziko la Edomu, ndi kuti, Aroni adzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wake; pakuti sadzalowa m’dziko limene ndapatsa ana a Israele, popeza munapikisana ndi mau anga ku madzi a Meriba. Tenga Aroni ndi Eleazara mwana wake, nukwere nao m’phiri la Hori; nuvule Aroni zovala zake, numveke Eleazara mwana wake; ndipo Aroni adzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wake, nadzafa komweko. Pamenepo Mose anachita monga adamulamula Yehova; ndipo anakwera m’phiri la Hori pamaso pa khamu lonse. Ndipo Mose anavula Aroni zovala zake, naveka Eleazara mwana wake; ndipo Aroni anafa pomwepo pamwamba paphiri. Pamenepo Mose ndi Eleazara anatsika m’phirimo. Pamene khamu lonse linaona kuti Aroni adamwalira, anamlira Aroni masiku makumi atatu, ndiyo mbumba yonse ya Israele.”
Mu Eksodo, Lamulo la God lalembedwa, kunena kuti ana a mkulu wansembe ayenera kupitiriza ntchito ya mkulu wansembe pamene afika msinkhu wokhwima, monga atate ao ankachitira.
Mu Eksodo 28:1-5, “Ndipo akuyandikire Aroni mbale wako, ndi ana ake aamuna pamodzi naye, mwa ana a Israele, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe, ndiwo Aroni, Nadabu, ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni. Ndipo usokere Aroni mbale wako zovala zopatulika, zikhale zaulemerero ndi zokoma. Ndipo ulankhule ndi onse a mtima waluso, amene ndawadzaza ndi (mzimu wa nzeru—NKJV), kuti amsokere Aroni zovala apatulidwe nazo, andichitire Ine ntchito ya nsembe. Ndipo zovala azisoka ndi izi: chapachifuwa ndi efodi, ndi mwinjiro, ndi malaya opikapika, ndi nduwira, ndi mpango; tero apangire Aroni mbale wako ndi ana ake zovala zopatulika, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe. Ndipo atenge golide, ndi lamadzi ndi lofiirira ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.”
God momveka bwino anadzodza Aroni, mkulu wake wa Mose, ku ntchito ya unsembe. Ntchito ya unsembe si makhala kwa munthu aliyense. Choncho, God analamula Mose kuti apatulire Aroni monga mkulu wansembe, ndi kumusokera iye zovala zoyera monga zinafotokozedwa ndi Iye. Ife sitiyenera kuiwala mau a God.
Komanso mu Eksodo 29:1-9, “(Ndipo ichi ndi chimene uchite kwa iwo kuti uwayeretse iwo kuti anditumikire Ine monga ansembe—NKJV) : tenga ng’ombe yamphongo, ndi nkhosa ziwiri zamphongo zangwiro, ndi mkate wopanda chotupitsa, ndi timitanda topanda chotupitsa tosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda chotupitsa, todzoza ndi mafuta; utipange ndi ufa wosalala watirigu. Ndipo uziike mu dengu limodzi, ndi kubwera nazo mudengu, pamodzi ndi ng’ombe yamphongo ndi nkhosa ziwiri zamphongo. Ndipo ubwere nao Aroni ndi ana ake aamuna ku khomo la chihema chokomanako, ndi kuwasambitsa m’madzi. Pamenepo utenge zovalazo ndi kuveka Aroni malaya am’kati, ndi mwinjiro wa efodi, ndi efodi, ndi chapachifuwa, ndi kummangira m’chuuno ndi mpango wa efodi woluka mwanzeru; ndipo uike nduwira pamutu pake, ndi kuika korona wopatulika panduwirapo. Pamenepo utenge mafuta odzoza nao nuwatsanulire pamutu pake, ndi kumdzoza. Ndipo ubwere nao ana ake aamuna ndi kuwaveka malaya am’kati. Uwamangirenso Aroni ndi ana ake aamuna mipango m’chuuno mwao, nuwamangire akapa pamutu pao; ndipo akhale ansembe mwa lemba losatha; (Choncho udzapereka Aroni ndi ana ake kukhala oyera.—NKJV)”.
“Uwamangirenso Aroni ndi ana ake aamuna mipango m’chuuno mwao, nuwamangire akapa pamutu pao; ndipo akhale ansembe mwa lemba losatha; (Choncho udzapereka Aroni ndi ana ake kukhala oyera.—NKJV)”. God analamula kuti Aroni ndi ana ake okha ayenera kupatulidwa kuti atumikire unsembe kosatha. Pamene Iye kwenikweni ananena kuti, “mwa lemba losatha,” linagwira ntchito ngakhale pamene Yesu anadza ku dziko lino lapansi.
Choncho Luka amafotokoza mwakuya kuti Zakariya anali mbadwa ya Aroni mkulu wansembe. Pamene Zakariya ankatumikira monga wansembe pamaso pa God m’kachisi wa Ambuye, mngelo anaonekera ndi kumuuza iye kuti pemphero lake linamveka; ndipo kuti mkazi wake Elisabeti adzamubalira iye mwana wamwamuna.
Zakariya sanakhulupirire zimenezi ndi kunena kuti, “Mkazi wanga ndi wokalamba, kodi iye angabale bwanji mwana?” Chifukwa cha kukaikira kwakwe, God anampanga iye kukhala wosalankhula kwa kanthawi kuti amuonetse kuti mau Ake anali oona.
Nthawi itakwana, mkazi wake anakhala ndi pakati ndipo patapita kanthawi, Mariya, namwali, anakhalanso ndi pakati. Zochitika ziwiri zonse zinali kukonzekera ntchito ya God ku chipulumutso chathu. Kuti apulumutse mtundu wa anthu owonongeka, Iye adayenera kutuma mtumiki Wake Yohane ndi kupanga Mwana Wake wobadwa yekha Yesu kubadwa m’dziko lino lapansi.
Choncho, God adapanga Mwana Wake kuti abatizidwe ndi Yohane ndi cholinga chakuti apereke machimo onse a dziko lapansi kuti iwo amene anakhulupirira mwa Iye adzapulumutsidwe.
Mwakugawa Chapadera cha God!
| Kodi God anakonza ndani patsogolo pa Yesu ku ntchito ya chiombolo? |
| Yohane Mbatizi |
God anakonza Yohabe kuti abadwe m’dziko lino lapansi Yesu asanabadwe. Yohane anabadwa kuti iye abatize Yesu ndi kupereka machimo onse a dziko lapansi pa Iye. Mbadwa ya mkulu wansembe inkayenera kupereka nsembe ya chitetezero ndi cholinga chakuti ikwaniritse Pangano la God limene linapangidwa m’Chipangano Chakale ndi Chatsopano; kuti Uthenga Wabwino wa chiombolo wa Yesu ukhulupiriridwe ndi kuchitidwa molondola.
Mu Eksodo, God anapatsa Israyeli Lamulo Lake ndi Mapangano; Lamulo la God komanso lamulo lotsogolera utumiki wa nsembe m’Chihema, mpaka zobvala za ansembe, tsatanetsatane wa nsembe, komanso kulowa m’malo kwa unsembe kwa ana a ansembe. God anasankha Aroni ndi mbadwa zake kuti akhale ansembe aukulu kwa muyaya.
Choncho, mbadwa zonse za Aroni zinkapereka nsembe ndipo akulu ansembe ankachokera kokha m’nyumba ya Aroni. Mukuona momwe zinalili?
Koma mwa mbadwa zambiri za Aroni, God anasankha wansembe wina dzina lake Zakariya ndi mkazi wake Elisabeti. Iye adanena kuti, “Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga.” Pamene God anauza Zakariya kuti Iye adzapanga Elisabeti kuti akhale ndi mwana, komanso kuti Iye anayenera kumutcha iye Yohane, iye anali odabwa kwambiri kotero kuti iye anakhala osalankhula pa kulamula Kwake mpaka pamene mwana anabadwa ndi kutchulidwa dzina.
Ndipo indedi, mwana anabadwa m’nyumba mwake. Pamene nthawi inafika kuti atchule dzina mwana malingana ndi mwambo wa Israyeli, iwo ankakonda kutchula dzina mwana dzina la atate wake.
“Ndipo inakwanira nthawi ya Elizabeti, ya kubala kwake, ndipo anabala mwana wamwamuna. Ndipo anansi ake ndi abale ake anamva kuti Ambuye anakulitsa chifundo chake pa iye; nakondwera naye pamodzi. Ndipo panali tsiku lachisanu ndi chitatu iwo anadza kudzadula kamwanako; ndipo akati amutche dzina la atate wake Zekariya. Ndipo amake anayankha, kuti, Iai; koma adzatchedwa Yohane. Ndipo iwo anati kwa iye, Palibe wina wa abale ako amene atchedwa dzina ili. Ndipo anakodola atate wake, afuna amutche dzina liti? Ndipo iye anafunsa cholemberapo, nalemba, kuti, Dzina lake ndi Yohane. Ndipo anazizwa onse. Ndipo pomwepo panatseguka pakamwa pake, ndi lilime lake linamasuka, ndipo iye analankhula, nalemekeza Mulungu(God). Ndipo panagwa mantha pa iwo onse akukhala oyandikana nao; ndipo analankhulalankhula nkhani izi zonse m’dziko lonse la mapiri a Yudeya. Ndipo onse amene anazimva anazisunga m’mtima mwao, nanena, Nanga mwana uyu adzakhala wotani? Pakuti dzanja la Ambuye linakhala pamodzi ndi iye.” (Luka 1:57-66).
Zakariya anali osalankhula nthawi imeneyo. Pamene nthawi inakwana yotchula dzina kamwanako, abale anapereka maganizo kuti mwanayo ayenera kukhala Zakariya. Koma amayi ake analimbikira kuti dzina lake liyenera kukhala Yohane. Pamene zimenezi, abale ananena kuti palibe amene ali ndi dzina limenelo m’banja ndipo kuti mwanayo ayenera kutchedwa dzina la atate wake.
Pamene Elisabeti anapitiriza kukakamira pa dzinalo, abale anapita kwa Zakariya ndi kumufunsa kuti dzina la mwana akhala ndani. Zakariya, amene anali osalankhulabe, anafunsa cholemberapo ndi kulemba kuti ‘Yohane’. Abale onse anazizwa pa kusankha kwa dzina kosazolowereka.
Koma pamene anatchula dzina, pakamwa pa Zakariya panatseguka nthawi yomweyo. Iye analemekeza God ndipo iye anadzadzidwa ndi Mzimu Woyera ndi kunenera.
Luka amatiuza ife za kubadwa kwa Yohane Mbatizi m’nyumba ya Zakariya. “Kunali munthu wansembe, dzina lake Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya.” Mu mwakugawa chapadera cha God, Yohane Mbatizi, woimirira wa mtundu wa anthu anabadwa kwa Zakariya, mbadwa ya Aroni.
Ndipo kudzera mwa Yohane Mbatizi ndi Yesu Kristu, God adatsiriza chipulumutso cha mtundu wa anthu. Ndife opulumutsidwa ku machimo athu onse pokhulupilira mu ntchito ya chiombolo yochitidwa kudzera mwa Yohane ndi Yesu Kristu.
Ubatizo wa Yesu
| Kodi ndi chifukwa chiyani Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi? |
| Kuti atenge machimo onse a dziko lapansi |
Yohane Mbatizi anachitira umboni kuti Yesu anali Mwana wa God ndipo Iye anachotsa machimo athu onse. Iye anali Yohane Mbatizi, mtumiki wa God amene anachitira umboni za chipulumutso chathu. Sizikutanthauza kuti God samatiuza ife Yekha kuti Iye ndi Mpulumutsi wathu. God amagwira ntchito kudzera mwa anthu Ake mu mpingo, komanso kudzera m’makamwa a anthu Ake onse amene apulumutsidwa.
God akunena kuti, “Munene inu zotonthoza mtima kwa Yerusalemu, nimufuulire kwa iye, kuti nkhondo yake yatha, kuti kuipa (mphulupulu) kwake kwakhululukidwa; kuti iye walandira mowirikiza m’dzanja la Yehova, chifukwa cha machimo ake onse. Udzu unyala, duwa lifota, koma mau a Mulungu(God) wathu adzakhala nthawi zachikhalire” (Yesaya 40:2, 8).
“Simulinso ochimwa. Ndatetezera machimo anu onse ndipo nkhondo yanu yatha.” Motero mau a Uthenga Wabwino wa chiombolo amapitiriza kufuura kwa ife. Uwu ndi omwe umatchedwa kuti uthenga okonzedwa.
Pamene ife tamvetsetsa ntchito ya Yohane Mbatizi, pamene ife kwenikweni tamvetsetsa kuti machimo onse a dziko lapansi anaperekedwa kwa Yesu kudzera mwa Yohane Mbatizi, ife tonse tingamasulidwe ku machimo athu.
Mabuku onse anayi a Uthenga Wabwino amatiuza ife za Yohane Mbatizi, ndipo mneneri wotsiriza wa Chipangano Chakale amachitiranso umboni za Yohane Mbatizi, mtumiki wa God. Ndipo Chipangano Chatsopano chimayamba ndi kubadwa kwa Yohane Mbatizi komanso kupereka kwa machimo kudzera mwa iye.
Nanga kodi ndi chifukwa chiyani ife timamutcha iye Yohane Mbatizi? Ndi chifukwa chakuti iye anabatiza Yesu. Kodi Ubatizo umatanthauza chiyani? Umatanthauza ‘Kupereka, Kukwiriridwa, Kutsukidwa’― chimodzimodzi ndi ‘kuika manja’ m’Chipangano Chakale.
Mchipangano Chakale, pamene munthu wachimwa, iye ankapereka machimo ake pa mutu wa chopereka cha uchimo, nsembe yopanda chirema, poika manja ake pa chopereka cha uchimo, ndipo nsembe inkafa ndi machimo amenewo. ‘Kuika manja’ kumatanthauza ‘Kupereka.’ Choncho, ‘Kuika manja’ ndi ‘Ubatizo’ zili ndi tanthauzo lofanana koma ndi maina osiyana.
Nanga kodi tanthauzo la Ubatizo wa Yesu linali chiyani? Ubatizo Wake unali njira yokhayo yopangira chitetezero mkati mwa lemba la God.
Mchipangano Chakale, ochimwa ankayenera kupereka manja ao pa mutu wa nsembe kuti apereke machimo ao pa mutu pake. Kenako iwo ankayenera kudula khosi lake ndipo ansembe ankabweretsa mwazi kuti aike uwo pa nyanga za guwa lansembe lopsereza. Iyi inali njira yotetezera machimo a tsiku ndi tsiku.
Nanga, kodi iwo ankatetezera bwanji machimo a pachaka?
Aroni, mkulu wansembe ankaperekera nsembe anthu onse a Israyeli. Chifukwa chakuti Yohane Mbatizi anabadwa m’nyumba ya Aroni, kunali koyenera kwa iye kukhala mkulu wansembe, ndipo God adampangiratu iye kuti akhale mkulu wansembe wotsiriza malingana ndi lonjezo Lake la chiombolo.
Yohane Mbatizi anali woimirira wa anthu onse komanso mkulu wansembe wotsiriza wa mtundu wonse wa anthu chifukwa chakuti Chipangano Chakale chinatha pamene Yesu Kristu anabadwa. Kodi winanso ndindani kuposa Yohane Mbatizi amene anapereka machimo onse a dziko lapansi pa Yesu m’Chipangano Chatsopano, monga Aroni ankatetezera machimo a anthu ake m’Chipangano Chakale? Monga mkulu wansembe wotsiriza m’Chipangano Chakale komanso woimirira wa mtundu wonse wa anthu, Yohane Mbatizi anasamutsira machimo onse a dziko lapansi pa Yesu pamene iye anam’batiza Iye.
Chifukwa chakuti Yohane anasamutsira uchimo onse kwa Yesu, ife tingapulumutsidwe pokhulupilira mu Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu. Yesu anakhala Mwanawankhosa kuti apulumutse ochimwa onse, motero kugwira ntchito ya chiombolo monga momwe God anakonzera. Yesu anatiuza ife kuti Yohane Mbatizi anali mneneri wotsiriza, mkulu wansembe wotsiriza amene anasamutsira machimo onse a dziko lapansi kwa Iye.
Kodi ndi chifukwa chiyani Yesu sanachite Yekha? Kodi ndi chifukwa chiyani Iye anafunika Yohane Mbatizi? Panali chifukwa chimene Yohane Mbatizi anabwerera miyezi isanu ndi umodzi Yesu asanabwere. Kunali kukwaniritsa Lamulo la Chipangano Chakale, kuti akwaniritse Chipangano Chakale.
Yesu anabadwa kwa namwali Mariya, ndipo Yohane Mbatizi anabadwa kwa mkazi wokalamba wotchedwa Elisabeti.
Izi zinali ntchito za God, ndipo Iye anakonza izo kuti apulumutse ochimwa onse. Kuti atipulumutse ife ku nkhondo yosatha yolimbana ndi uchimo, komanso mazunzo onse a mtundu wa anthu wa uchimo, Iye anatuma mtumiki Wake Yohane, ndipo kenako Mwana Wake Yesu. Yohane Mbatizi anatumidwa monga woimirira wa mtundu wonse wa anthu, mkulu wansembe wotsiriza.
Munthu Wamkulu Koposa Wakubadwa Mwa Mkazi
| Kodi munthu wamkuru anali ndani pa dziko lapansi? |
| Yohane Mbatizi |
Tiyeni tione pa Mateyu 11:7-14. “Ndipo m’mene iwo analikumuka, Yesu anayambonena ndi makamu a anthu za kwa Yohane, Munatuluka kunka kuchipululu kukapenyanji? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi? Koma munatuluka kukaona chiyani? Munthu wovala zofewa kodi? Onani, akuvala zofewa ali m’nyumba zamafumu. Koma munatulukiranji? Kukaona mneneri kodi? Indetu, ndinena kwa inu, wakuposa mneneri. Uyu ndiye amene kunalembedwa za iye, kuti, Onani Ine nditumiza mthenga wanga pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu m’tsogolo mwanu. Indetu ndinena kwa inu, Sanauke wakubadwa mwa mkazi munthu wamkulu woposa Yohane Mbatizi; koma iye amene ali wochepa mu Ufumu wa Kumwamba amkulira iye. Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa Kumwamba uli wokakamizidwa, ndipo okakamirawo aukwatula ndi mphamvu. Pakuti aneneri onse ndi chilamulo chinanenera kufikira pa Yohane. Ndipo ngati mufuna kulandira, uyu ndiye Eliya amene amati akudza.”
Anthu anapita kuchipululu kukaona Yohane Mbatizi, amene anafuula kuti, “Lapani, ana a njoka inu!” Ndipo Yesu ananena kuti, “Koma munatuluka kukaona chiyani? Munthu wovala zofewa kodi? Onani, akuvala zofewa ali m’nyumba zamafumu.”
Yesu Mwini anachitira umboni za ukuru wa Yohane. “Kodi munapita kukapenyanji? Wankhanza amene amavala ubweya wa ngamila ndi kufuula pamwamba pa mapapo ake? Iye ayenera kuti wavala ubweya wa ngamila. Koma munaturuka kukaona chiani? Munthu wovala zofewa kodi? Iwo akuvala zofewa ali m’nyumba zamafumu. Koma iye ndi wamkuru kuposa mfumu,” anachitira umboni Yesu. “Onani, akuvala zofewa ali m’nyumba zamafumu. Koma munatulukiranji? Kukaona mneneri kodi? Indetu, ndinena kwa inu, wakuposa mneneri.”
M’masiku akale, aneneri anali aakulu kuposa mafumu. Yohane Mbatizi anali woposa mfumu, komanso woposa mneneri. Iye anali woposa aneneri onse a m’Chipangano Chakale Kwenikweni, Yohane, mkulu wansembe wotsiriza komanso woimirira wa mtundu wa anthu, anali woposa Aroni mkulu wansembe woyamba. Yesu Mwini anachitira umboni za Yohane.
Kodi woimirira wa mtundu wa anthu ndindani? Kupatula Kristu Mwini, kodi munthu wamkuru pa dziko lapansi ndindani? Yohane Mbatizi. “Ndinena kwa inu, wakuposa mneneri. Uyu ndiye amene kunalembedwa za iye, kuti, Onani Ine nditumiza mthenga wanga pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu m’tsogolo mwanu.”
Yohane Mbatizi anachitira umboni kuti nkhondo yolimbana ndi uchimo yatha. “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu(God) amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!” Anali Yohane Mbatizi amene anachitira umboni kuti Yesu anachotsa machimo machimo a dziko lapansi.
Mu Mateyu 11:11, “Indetu ndinena kwa inu, Sanauke wakubadwa mwa mkazi munthu wamkulu woposa Yohane Mbatizi.” Kodi pakhalapo wina wamkuru woposa Yohane Mbatizi wakubadwa mwa akazi?
Kodi zikutanthauza chiyani kuti wakubadwa mwa ‘mkazi’? Zikutanthauza mtundu wonse wa anthu. Kupatula Adamu, mtundu wonse wa anthu unabadwa mwa akazi. Inde, sanauke wakubadwa mwa akazi munthu wamkuru woposa Yohane Mbatizi. Choncho, iye ndi mkulu wansembe wotsiriza komanso woimirira wa mtundu wa anthu. Yohane Mbatizi anali mkulu wansembe, mneneri, komanso woimirira wathu.
Mchipangano Chakale, Aroni ndi ana ake anadzodzedwa ndi God kuti atumikire kwamuyaya. Machimo onse ankayenera kutsukidwa kudzera mwa Aroni ndi ana ake Zinali monga God analamulira.
Ngati winawake pakati pa Alevi wadza kutsogolo ndi kuyerekeza kuchita ntchito imeneyi, iye akanafa pomwepo. Zonse zimene iwo ankachita kunali kusaka nkhuni zokolezera moto pa guwa, kusenda nyama, kukonza matumbo, ndi kuchotsa mafuta. Ngati iwo adali odzikuza kwambiri kuyesa kuchita ntchito ya ansembe, iwo akanafa chabe. Ndi Lamulo la God. Iwo sakanadutsa mzere.
Pa dziko lapansi, sipanauke munthu wamkuru woposa Yohane Mbatizi. Iye anali wamkuru mwa onse amene sakhala kwa muyaya. “Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa Kumwamba uli wokakamizidwa, ndipo okakamirawo aukwatula ndi mphamvu” (Mateyu 11:12).
Chiombolo cha mtundu wa anthu chinakwaniritsidwa pamene Yohane Mbatizi anabatiza Yesu, ndipo iwo amene amakhulupilira mwa Yesu angalowe mu ufumu wa Kumwamba. Iwo amakhala olungama. Tiyeni tione momwe atate wa Yohane anachitira umboni za mwana wake.
Umboni wa Zakariya, Atate wa Yohane
| Kodi Zakariya ananenera chiani za mwana wake? |
| Yohane adzakonza njira ya Ambuye popereka chidziwitso cha chipulumutso kwa anthu Ake. |
Tiyeni tiwerenge Luka 1:67-80. “Ndipo atate wake Zekariya anadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nanenera za Mulungu(God), nati, Wolemekezeka Ambuye, Mulungu(God) wa Israele; chifukwa Iye anayang’ana, nachitira anthu ake chiombolo. Ndipo Iye anatikwezera ife nyanga ya chipulumutso, mwa fuko la Davide mwana wake. Monga Iye analankhula ndi m’kamwa mwa aneneri ake oyera mtima, akale lomwe, hipulumutso cha adani athu, ndi padzanja la anthu onse amene atida ife. Kuchitira atate athu chifundo, ndi kukumbukira pangano lake lopatulika; chilumbiro chimene Iye anachilumbira kwa Abrahamu atate wathu. Kutipatsa ife kuti titalanditsidwa kudzanja la adani athu, tidzamtumikira Iye, opanda mantha, m’chiyero ndi chilungamo pamaso pake, masiku athu onse. Eya, ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa mneneri wa Wamkulukulu; pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zake. Kuwapatsa anthu ake adziwitse chipulumutso, ndi makhululukidwe a machimo ao (kutsuka machimo), chifukwa cha mtima wachifundo wa Mulungu(God) wathu. M’menemo mbandakucha wa kumwamba udzatichezera ife. Kuwalitsira iwo okhala mumdima ndi mthunzi wa imfa; kulunjikitsa mapazi athu mu njira ya mtendere. Ndipo mwanayo anakula, nalimbika mu mzimu wake, ndipo iye anali m’mapululu, kufikira masiku akudzionetsa yekha kwa Israele.”
Zakariya ananenera zinthu ziwiri. Iye ananenera kuti Mfumu ya anthu onse yadza. Kuchokera mu ndime 68 mpaka 73, iye ananenera ndi chisangalalo kuti God sanaiwale malonjezo Ake ndipo kuti Yesu, monga momwe God analonjezera kwa Abrahamu, anabadwa kwa namwali Mariya kuti apulumutse mbadwa zake m’manja mwa adani awo.
Ndipo kuchokera mu ndime ya 74 akuti, “Kutipatsa ife kuti titalanditsidwa kudzanja la adani athu, tidzamtumikira Iye, opanda mantha.” Ichi ndi chikumbutso cha Lonjezo la God kwa Abrahamu ndi anthu a Israyeli, ndipo iye ananenera. “Kutipatsa ife kuti tidzamtumikira Iye, opanda mantha.”
Kuchokera mu 76, iye ananenera za mwana wake. “Eya, ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa mneneri wa Wamkulukulu; pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zake. Kuwapatsa anthu ake adziwitse chipulumutso, ndi makhululukidwe a machimo ao (kutsuka machimo), chifukwa cha mtima wachifundo wa Mulungu(God) wathu. M’menemo mbandakucha wa kumwamba udzatichezera ife. Kuwalitsira iwo okhala mumdima ndi mthunzi wa imfa; kulunjikitsa mapazi athu mu njira ya mtendere.”
Apa iye ananena kuti, “Kuwapatsa anthu ake adziwitse chipulumutso, ndi makhululukidwe a machimo ao (kutsuka machimo).” Kodi ndi kudzera kwa ndani kumene iye ananena kuti chidziwitso cha chipulumutso chidzaperekedwa? Yohane Mbatizi. Kodi inu mukuona zonse zimenezi? Yohane Mbatizi, kudzera m’mau a God, amayenera kutipatsa ife chidziwitso kuti Yesu ndi Mwana wa God amene anachotsa machimo a dziko lapansi.
Tsopano, tiyeni tione pa Marko 1. “Chiyambi chake cha Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu(God). Monga mwalembedwa mu Yesaya mneneri, Ona, ndituma mthenga wanga patsogolo pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu. Mau a wofuula m’chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake. Yohane anadza nabatiza m’chipululu, nalalikira Ubatizo wa kutembenuka mtima wakuloza ku chikhululukiro (kuchotsa machimo) cha machimo. Ndipo anatuluka a ku dziko lonse la Yudeya, ndi a ku Yerusalemu onse, nadza kwa iye nabatizidwa ndi iye mumtsinje Yordani, powulula machimo ao.” (Marko 1:1-5)
Pamene Aisrayeli anamva kuchokera kwa Yohane Mbatizi, iwo anasiya kupembedza mafano a Achikunja ndipo anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Koma Yohane anachitira umboni kuti, “Ine ndikubatizani inu ndi madzi kuti mubwerere kwa God. Koma Mwana wa God azadza ndi kubatizidwa ndi ine kuti machimo anu onse aperekedwe pa Iye. Ndipo ngati inu mukhulupirire mu Ubatizo Wake monga momwe mukubatizidwira ndi ine, machimo anu onse adzaperekedwa pa Iye, monga momwe machimo amaperekedwa kudzera mu kuika manja m’Chipangano Chakale.” Izo ndi zomwe Yohane Mbatizi anachitira umboni.
Choona chakuti Yesu anabatizidwa mu Yordano chikutanthauza kuti Iye anabatizidwa mu mtsinje wa imfa. Ife timaimba pa maliro kuti, “♪M’chimwemwe pang’ono ndi pang’ono, ife tidzakumana m’mbali mwa mtsinje wokongola. Ife tidzakumana m’mbali mwa mtsinje wa wokongola.♪” Ife tikafa, tidzaoloka Mtsinje wa Yordano. Mtsinje wa Yordano ndi mtsinje wa imfa. Yesu anabatizidwa mu mtsinje wa imfa.
Ubatizo Umene Anasamutsira Machimo Athu
| Kodi ‘kuika manja’ m’Chipangano Chatsopano ndi chiani? |
| Ubatizo wa Yesu |
Mu Mateyu 3:13-17, ife timawerenga kuti, “Pamenepo Yesu anachokera ku Galileya nadza ku Yordani kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye. Koma Yohane anati amkanize, nanena, Ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi? Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero. Pamenepo anamlola Iye. Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anatuluka m’madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu(God) wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye; ndipo onani, mau akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.”
Yesu anadza ku Yordano ndipo anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. “Ndibatize Ine.” Ndipo Yohane, ananena kuti, “Ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi?” Mkulu wansembe wa kumwamba ndi wa dziko lapansi anakumana pamodzi.
Malingana ndi Ahebri, Yesu Kristu ndi Mkulu Wansembe kwamuyaya monga mwa dongosolo la Melikizedeke. Iye ndi opanda m’badwo. Iye si mbadwa ya Aroni, ngakhalenso munthu aliyense pa dziko lapansi. Iye ndi Mwana wa God, Mlengi wathu. Choncho, Iye alibe m’badwo. Koma Iye anataya ulemelero wa kumwamba ndi kudza ku dziko lapansi kudzapulumutsa anthu Ake.
Chifukwa chimene Iye anatsikira ku dziko lino lapansi chinali kuti apulumutse ochimwa onse amene anavutika ndi chinyengo cha Satana. Kuwonjezera apo, Iye anachotsa machimo onse a dziko lapansi pobatizidwa ndi Yohane Mbatizi. “Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero. Pamenepo anamlola Iye.”
“Balola tsopano.” Balola! Yesu analamula woimirira wa mtundu wonse wa anthu ndi kugwetsa mutu Wake. Mchipangano Chakale, pamene nsembe inkaperekedwa kwa God, wochimwa kapena mkulu wansembe ankaika manja ake pa mutu pake ndi kupereka machimo. ‘Kuika manja a munthu pa mutu’ kumatanthauza ‘Kupereka.’
Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Chimene chinkatanthauza chinali chimodzimodzi ndi kuika manja m’Chipangano Chakale. ‘Kupereka,’ ‘Kukwiriridwa,’ ‘Kutsukidwa,’ komanso ‘Kupereka nsembe’ ndi chimodzimodzinso. Chipangano Chatsopano ndi zenizeni pamene Chipangano Chakale ndi chithunzithunzi chake.
Pamene wochimwa waika manja ake pa mwanawankhosa m’Chipangano Chakale, uchimo wake unkaperekedwa pa mwanawankhosa ndipo mwanawankhosayo ankafa. Pamene mwanawankhosa wafa, iye ankakwiriridwa. Uchimo wa munthu amene ankaika manja ake pa mwanawankhosa unkaperekedwa pa mwanawankhosa kuti mwanawankhosayo afe ndi uchimo! Pamene uchimo unkaperekedwa pa mwanawankhosa, kodi munthu amene ankabweretsa mwanawankhosayo ankakhalanso opanda uchimo?
Tiyeni tiyerekeze kuti kampango kopukutira thukutaka ndi uchimo ndipo chinkuza mauchi ndi mwanawankhosa. Ndipo ndikaika manja anga pa chinkuza mauchi, uchimo umenewu uperekedwa pa chinkuza mauchi, mwanawankhosa. God Mwini anasankha kuti zikhale choncho. “Ikani manja anu.” Choncho kuti aomboledwe ku machimo, munthu ayenera kuika manja ake. Akatero, ndiye kuti iye alibe uchimo. Ubatizo wa Yesu ndi wotsuka, kukwirira, komanso kupereka uchimo pa Iye. Ndi ndendende zomwe zimatanthauza.
| Kodi chikutanthauza chiyani kukwaniritsa chilungamo chonse? |
| Ndi kutsuka machimo onse popereka machimo pa Yesu. |
Nanga pamene Yesu anabatizidwa kuti achotse machimo onse a dziko lapansi, kodi iwo onse indedi anaperekedwa pa Iye? Machimo onse a dziko lapansi anaperekedwa pa Yesu ndipo anthu onse anaomboledwa. Ndi chimodzimodzi ndi kupereka kwa machimo ku nsembe m’Chipangano Chakale. Yesu anadza ku dziko lino lapansi ndipo pa Yordano, Iye ananena kuti, “Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero. Pamenepo anamlola Iye” (Mateyu 3:15).
Kenako, Yohane anabatiza Yesu. Yesu anauza Yohane kuti kunali koyenera kwa iwo kukwaniritsa chilungamo chonse ndi Ubatizo Wake. ‘Chilungamo chonse’ chimatanthauza ‘moyenera kwambiri ndi mokwanira.’ ‘Motero’ kunali koyenera iwo kukwaniritsa chilungamo chonse. Zimenezi zikutanthuza kuti kunali koyenera kwa Yohane kubatiza Yesu, ndipo Yesu kubatizidwa ndi Yohane, kuti apereke machimo onse a dziko lapansi pa Yesu.
God amapereka chiombolo potengera ndi Ubatizo wa Yesu, kudzipereka nsembe Kwake, ndi chikhulupiriro chathu. “Mtundu wonse wa anthu ukuvutika ndi uchimo ndipo ukuzunzidwa ndi mdierekezi chifukwa cha uchimo wake. Choncho, cholinga chakuti iwo apulumutsidwe ndi kutumidwa kumwamba, iwe, monga woimirira wa mtundu wa anthu komanso mbadwa ya Aroni, uyenera kundibatiza Ine chifukwa cha anthu onse. Ndiyenera kubatizidwa ndi iwe. Kenako ntchito ya chiombolo idzakwaniritsidwa.”
Kenako iye analola.
Choncho Yohane anabatiza Yesu. Iye anaika manja ake pa mutu wa Yesu ndi kupereka machimo onse a dziko lapansi pa Yesu. Yesu anali Mpulumutsi amene anatsuka machimo athu onse. Ndife opulumutsidwa pokhulupilira mu chiombolo Chake. Kodi inu mukukhulupirira?
Pambuyo pa Ubatizo Wake, ntchito yoyamba ya Yesu mu utumiki Wake wapoyera pa Yordano kudzera m’manja a woimirira wa mtundu wonse wa anthu, Iye anayendayenda polalikira Uthenga Wabwino kwa zaka zitatu ndi theka ali ndi machimo onse a dziko lapansi pa mutu Pake.
Iye anauza mkazi amene anagwidwa m’chigololo kuti, “Inenso sindikutsutsa iwe.” Iye sakanamutsutsa iye chifukwa chakuti Iye adatenga machimo ake onse pa Iye Mwini ndipo amafuna kufa pa Mtanda chifukwa cha iwo. Pamene Iye ankapemphera pa malo otchedwa Getsemane, Iye anapemphera katatu kuchondelera Atate kuti alole chikho chimupitirire Iye, koma mofulumira anasiya ndi kunena kuti, “koma si kufuna kwanga ai, komatu kwanu kuchitike” (Luka 22:42).
“Onani Mwanawankhosa wa God amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!”
| Kodi ndi machimo angati amene Yesu anachotsa? |
| Machimo onse a dziko lapansi |
Mu Yohane 1:29, “M’mawa mwake anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu(God) amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!” Yohane Mbatizi anabatiza Yesu. Ndipo tsiku lotsatira, Yesu anadza molunjika iye, anafuula, ndi kuchitira umboni kwa anthu. “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu(God) amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!”
Mwana wa God anadza ku dziko lino lapansi ndi kuchotsa machimo onse a dziko lapansi. Yohane Mbatizi anachitiranso umboni. Mu Yohane 1:35-36, “M’mawa mwakenso analikuimirira Yohane ndi awiri a ophunzira ake; ndipo poyang’ana Yesu alikuyenda, anati, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu(God)!”
Mwanawankhosa wa God amatanthauza kuti Iye ndi oona komanso kukhalapo kwenikweni kwa nsembe ya Chipangano Chakale, imene inkafa chifukwa cha machimo a Israyeli. Kwa inu ndi ine, Mwana wa God, Mlengi wathu, anadza ku dziko lino lapansi ndi kuchotsa machimo athu onse; machimo onse kuyambira ku chilengedwe cha dziko lapansi mpaka tsiku limene lidzatha, kuyambira uchimo oyambirira mpaka mphulupulu zathu, kuyambira zoperewera zathu mpaka zolakwa zathu. Iye anatiombola ife tonse ndi Ubatizo Wake ndi mwazi Wake pa Mtanda.
Yesu anachotsa machimo athu onse ndi kutipatsa ife chiombolo. Kodi mukumvetsetsa zimenezi? “Mwanawankhosa wa Mulungu(God) amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!”
Patha pafupifupi zaka 2000. Zikutanthauza kuti pafupifupi zaka 2000 zadutsa kuchokera pamene Iye anadza ku dziko lino lapansi. Ndipo mu 30 A.D., Yesu anachotsa machimo onse a dziko lapansi. Chaka cha 1 A.D. ndi chaka chimene Yesu anabadwa. Ife timatcha nthawi Kristu asanabwere kuti B.C. Choncho, pafupifupi zaka 2000 zadutsa kuchokera pamene Yesu anadza ku dziko lino lapansi.
Mu 30 A.D., Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Ndipo tsiku lotsatira, Yohane anafuula kwa anthu kuti, “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu(God) amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!”. “Onani!” Iye ankauza anthu kuti akhulupirire mwa Yesu, amene wachotsa machimo ao onse. Iye ankachitira umboni kuti Yesu anali Mwanawankhosa wa God, Iye amene anatipulumutsa ife ku machimo anthu onse.
Yesu anachotsa machimo athu onse ndi kuthetsa nkhondo yathu yosatha yolimbana ndi uchimo. Ndife tsopano opanda uchimo popeza Mwana wa God anachotsa machimo athu onse. Yohane Mbatizi anachitira umboni kuti Iye anachotsa machimo athu onse, machimo a inu ndi ine. “Iyeyu anadza mwa umboni kudzachita umboni za kuunikaku, kuti onse akakhulupirire mwa iye” (Yohane 1:7).
Popanda umboni wa Yohane, kodi ife tikanadziwa bwanji kuti Yesu anachotsa machimo athu onse? Baibulo limatiuza ife kawirikawiri kuti Iye anatifera ife, koma pa nthawi imeneyi, anali Yohane Mbatizi yekha amene anachitira umboni kuti Iye anachotsa machimo athu onse.
| Kodi ndi uchimo ochuruka bwanji uchimo wa dziko lapansi? |
| Machimo onse a anthu kuyambira kuchiyambi mpaka kumapeto a dziko lapansi |
Ambiri anachitira umboni pambuyo pa imfa ya Yesu, koma Yohane yekha anachitira umboni pamene Iye anali moyo. Kumene, ophunzira a Yesu anachitiranso umboni za chiombolo cha Yesu. Iwo anachitira umboni kuti Yesu anachotsa machimo athu, kuti Iye ndi Mpulumutsi wathu.
Yesu anachotsa tchimo la dziko lapansi. Tsopano, inu simunakwanitse zaka 100, sichoncho? Yesu anachotsa tchimo la dziko lapansi pamene Iye anali ndi zaka 30. Tsopano, lingalirani chithunzi ichi.
Tiyeni tiyerekeze kuti zinali zaka 4000 Yesu asanabwere. Ndipo kwatha zaka zopitirira 2000 kuchokera pamene Yesu anadza. Ife sitikudziwa kuti ilo lidzakhala motalika bwanji, koma mapeto adzabweradi. Iye akuti, “Ine ndine Alefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza, Chiyambi ndi Chitsiriziro” (Chivumbulutso 22:13).
Choncho padzakhaladi mapeto. Ndipo tili pa nthawi imene tikuyandikira chaka cha 2024. Kristu anachotsa machimo athu mu 30 A.D., ndipo zinali zaka 3 Iye asanafe pa Mtanda.
“Onani Mwanawankhosa wa Mulungu(God) amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!” Iye anachotsa tchimo la dziko lapansi, machimo a inu ndi ine. Pafupifupi zaka 2000 zadutsa kuchokera pamene Yesu anabadwa. Ife tsopano tikukhala pafupifupi zaka 2000 pamene Yesu anachotsa machimo athu. Ndipo ife tikukhalabe ndi moyo ndi kuchimwa m’masiku ano. Yesu ndi Mwanawankhosa wa God amene anachotsa tchimo la dziko lapansi. Ife timayamba kukhala m’dziko lino lapansi kuchokera pamene ife tabadwa.
Kodi ife tonse timachimwa kuchokera nthawi imene ife tabadwa, kapena sitichimwa? ―Ife timachimwa.― Tiyeni tidutse mu ndondomeko yonse. Kuchokera tsiku lomwe ife tabadwa kufika pamene ife tili ndi zaka 10, kodi ife timachimwa, kapena sitichimwa? ―Ife timachimwa.― Ndiye kodi machimo amenewo anaperekedwa pa Yesu kapena ai? ―Iwo anaperekedwa.― Chifukwa chakuti machimo onse anaperekedwa pa Yesu, Iye ndi Mpulumutsi wathu. Ngati sichoncho, kodi Iye akanakhala bwanji Mpulumutsi wathu? Machimo onse anaperekedwa pa Yesu.
Kuchokera zaka 11 mpaka 20, kodi ife timachimwa, kapena sitichimwa? Ife timachimwa m’mitima mwathu, m’machitidwe athu. Ndife akatswiri pa izo. Ife taphunzitsidwa kuti tisamachimwe, koma ife timachita uwo mosavuta kwambiri.
Ndipo God amatiuza ife kuti machimo amenewo anaperekedwa pa Yesu. Iye ankadziwa chomwe ife tinali, choncho Iye anachotseratu machimo amenewo.
Ndipo kodi kawirikawiri ife timakhala motalika bwanji m’dziko lino lapansi? Tiyeni tinene kuti ndi pafupifupi zaka 70. Ngati ife taphatikiza pamodzi machimo onse amene ife timachita mu zaka 70 zimenezo, kodi kulemera kwake kungakhale kotani? Ngati ife tingawalongedze iwo m’galimoto lolemera matani 8, mwina iwo angakhale magalimoto onyamula katundu opitirira 100.
Tangoyesani kuganizira kuti ndi uchimo ochuruka bwanji umene ife tidzachita m’moyo wathu wonse. Kodi machimo amenewo ndi a dziko lapansi, kapena si a dziko lapansi? Iwo ndi machimo a dziko lapansi. Ife timachimwa kuchokera pamene tabadwa, mpaka zaka 10, 10 mpaka zaka 20, 20 mpaka zaka 30... kufikira tsiku lomwe ife tidzafa, koma machimo onse amenewo aphatikidwa m’machimo a dziko lapansi amene aperekedwa kale pa Yesu kudzera mu Ubatizo Wake.
Mpulumutsi wa Munthu, Yesu Kristu
| Kodi Yesu anachotsa uchimo ochuruka bwanji? |
| Machimo onse a makolo athu, a ife komanso a mbadwa zathu, mpaka mapeto a dziko lapansi |
Yesu akutiuza ife kuti Iye anatsuka machimo onse amenewo. Popeza Yesu sakanadzibatiza Yekha, God anatuma mtumiki Wake Yohane patsogolo, woimirira wosankhidwa wa anthu onse. “Ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu(God) wamphamvu” (Yesaya 9:6). Mwa Iye Yekha, ndi mzeru Yake, mwa uphungu Wake, Iye anatuma woimirira wa mtundu wa anthu patsogolo, ndipo Mwini, Mwana wa God, anadza m’thupi ndi kuchotsa machimo onse a dziko lapansi kudzera mu Ubatizo wopatsidwa ndi Yohane Mbatizi. Kodi chimenechi si chipulumutso chodabwitsa?
Ndi zodabwitsa, sichoncho? Choncho, kamodzi kokha, pongobatizidwa ndi Yohane Mbatizi, Iye anatsuka machimo onse a anthu m’dziko lonse lapansi ndi kupulumutsa aliyense ku uchimo popachikidwa. Iye anatipulumutsa ife tonse. Ganizirani izo. Machimo anu onse kuchokera muli ndi zaka 20 mpaka zaka 30, 30 mpaka zaka 40, 40 mpaka zaka 60, mpaka zaka 70, mpaka zaka 100, komanso kuli iwo a ana anu. Kodi Iye anafafaniza machimo anu onse, kapena Iye sanatero? Inde, Iye anafafaniza. Iye ndi Yesu Kristu, Mpulumutsi wa mtundu wa anthu.
Chifukwa chakuti Yohane Mbatizi anasamutsira machimo athu onse kwa Yesu, komanso chifukwa chakuti God anakonza izo choncho, ife tingapulumutsidwe pokhulupilira mwa Yesu. Kodi inu ndi ine ndife ochimwa? Kodi machimo athu onse anaperekedwa pa Yesu kapena ai? ―si ifenso ochimwa, ndipo machimo athu anaperekedwa onse pa Yesu.―
Kodi ndindani angayerekeze kunena kuti muli uchimo m’dziko lino lapansi? Yesu anachotsa machimo onse a dziko lapansi. Iye anadziwa kuti ife tidzachimwa, ndipo anachotsanso machimo onse a m’tsogolo. Ena a ife ndife opitirira zaka 50 ndipo ena sitinakhale ngakhale theka la miyoyo yathu, koma timakamba za ife eni, kuphatikiza ine mwini, monga ngati kuti ife takhala kwa muyaya.
Pali ambiri a ife amene timakhala miyoyo ya chisokonezo. Ndiloleni ndi fotokoze m’njira iyi. Kodi theka la moyo wa ntchentche ndi wautali bwanji? Ndi pafupifupi maora 12 .
“God wanga! Ndinakumana ndi munthu otero ndi otero, ndipo iye anandimenya ndi chophera zouluka, ndipo pang’onong’ono ndikanafa, ndipo mukudziwa.” Iye wakhala kokha maora 12 ndipo sakanasiya kulankhula. Koma ilo linali kale theka la moyo wake.
Pofika 7 kapena 8 madzulo, iye amakumana ndi mathero a moyo wake, ndipo mu nthawi yochepa chabe, imfa. Zina zimakhala kwa maora 20, zina maora 21, ndipo zina zimakhala mpaka kukalamba maora 24. Izo zingalankhule za zokumana nazo za moyo wao wonse, koma kodi zimaoneka bwanji kwa ife? Pamene ife timakhala zaka 70 kapena 80, ife tinganene kuti, “Osandiseketsa.” Zokumana nazo zao ndi zopanda ntchito konse m’maso mwathu.
God ndi wamuyaya. Iye amakhala kwa muyaya. Iye amasankha chiyambi ndi mathero. Pamene Iye amakhala kwa muyaya, Iye amakhala mu nthawi ya muyaya. Iye amatiyang’ana ife kuchera pa malo Ake a muyaya.
Kakekalelo, Iye anachotsa machimo onse a dziko lapansi, kufa pa Mtanda, ndi kunenena kuti, “Kwatha.” Iye anauka patatha masiku 3 ndi kupita kumwamba. Iye tsopano amakhala kwa muyaya. Tsopano, Iye akuyang’ana pa aliyense wa ife.
Ndipo munthu m’modzi amanena kuti, “Oh, wokondedwa, ndachimwa kwambiri. Ngakhale ndakhala kokha zaka 20, ndachimwa kwambiri.” “Ndakhala kwa zaka 30 ndipo ndachimwa kwambiri. Zanyanya. Kodi ndi ndingakhululukidwe bwanji?”
Koma Ambuye wathu mu umuyaya Wake adzanena kuti, “Osandiseketsa. Sindinaombole kokha machimo ako kufikira tsopano, koma machimonso a makolo ako iwe usanabadwe, komanso machimo a mibadwo yonse ya mbadwa zako amene adzakhala pambuyo pa imfa yako.” Iye amanena zimenezi kwa inu kuchokera mu nthawi ya muyaya. Kodi inu mukhulupirira zimenezi? Khulupirira izo. Ndipo landirani mphatso ya chipulumutso yopatsidwa mwaulere kwa inu. Ndi kulowa mu ufumu wa kumwamba.
Tisakhulupirire m’malingaliro athu, koma m’mau a God. ‘Pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero.’ Chilungamo Chonse chinakwaniritsidwa kale ndi Mwanawankhosa wa God, amene anachotsa tchimo la dziko lapansi. Yesu anachotsa machimo onse a dziko lapansi. Kodi Iye anatero, kapena Iye sanatero? Iye anatero.
| Kodi Yesu ananena chiyani kumapeto pa Mtanda? |
| “Kwatha.” |
Yesu anachotsa machimo onse a dziko lapansi, anagamulidwa ku imfa m’bwalo la Pontiyo Pilato, ndipo anapachikidwa pa Mtanda.
“Ndipo anasenza mtanda yekha, natuluka kunka kumalo otchedwa Malo a Bade, amene atchedwa mu Chihebri, Gologota: kumene anampachika Iye; ndipo pamodzi ndi Iye awiri ena, chakuno ndi chauko, koma Yesu pakati. Koma Pilato analemba lembo, naliika pamtanda. Koma panalembedwa, YESU MNAZARAYO, MFUMU YA AYUDA. Ndipo lembo ilo analiwerenga ambiri a Ayuda; chifukwa malo amene Yesu anapachikidwapo anali pafupi pa mzindawo; ndipo linalembedwa mu Chihebri, ndi mu Chilatini, ndi mu Chigriki” (Yohane 19:17-20).
Tiyeni tione zimene zinachitika pamene Iye anapachikidwa pa Mtanda. “Chitapita ichi Yesu, podziwa kuti zonse zidatha pomwepo kuti lembo likwaniridwe.” Iye adatenga machimo athu onse malingana ndi Malemba. Iye anati, “Ananena, Ndimva ludzu. Kunaikidwako chotengera chodzala ndi vinyo wosasayo pa phesi la hisope, nachifikitsa kukamwa kwake. Pamene Yesu tsono adalandira vinyo wosasayo anati, Kwatha; ndipo anawerama mutu, napereka mzimu” (Yohane 19:28-30).
Pamene Iye adalandira vinyo wosasa, Iye ananena kuti, “Kwatha!” ndi kugwetsa mutu Wake ndi kupereka mzimu Wake. Iye anafa. Ndipo Yesu Kristu anauka patatha masiku 3 ndi kukwera kumwamba.
Tiyeni titembenukire ku Ahebri 10:1-9. “Pakuti chilamulo, pokhala nao mthunzi wa zokoma zilinkudza, osati chifaniziro chenicheni cha zinthuzo, sichikhozatu, ndi nsembe zomwezi chaka ndi chaka, zimene azipereka kosalekeza, kuwayesera angwiro iwo akuyandikira. Pakadapanda kutero, kodi sakadaleka kuzipereka, chifukwa otumikirawo sakadakhala nacho chikumbumtima cha machimo, popeza adayeretsedwa kamodzi? Komatu mu izizo muli chikumbukiro cha machimo chaka ndi chaka. Pakuti sikutheka kuti mwazi wa ng’ombe zamphongo, ndi mbuzi ukachotsera machimo. Mwa ichi polowa m’dziko lapansi, anena, Nsembe ndi chopereka simunazifune, koma thupi munandikonzera Ine. Nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo simunakondwere nazo; pamenepo ndinati, Taonani, ndafika, (Pamutu pake pa buku palembedwa za Ine) kudzachita chifuniro chanu, Mulungu(God). Pakunena pamwamba apa, kuti, Nsembe ndi zopereka ndi nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo simunazifune, kapena kukondwera nazo (zimene ziperekedwa monga mwa Lamulo), pamenepo anati, Taonani, ndafika kudzachita chifuniro chanu. Achotsa choyambacho, kuti akaike chachiwiricho.”
Chiombolo Cha Muyaya
| Kodi ife tingathetse bwanji vuto la uchimo wa tsiku ndi tsiku pambuyo pokhulupilira mwa Yesu? |
| Potsimikira kuti Yesu wafafaniza kale uchimo onse kudzera mu Ubatizo Wake |
Lamulo linali mthunzi wa zokoma zirinkudza. Nsembe za chipangano Chakale, za nkhosa ndi mbuzi, zinavumbulutsa kwa ife kuti Yesu Kristu azadza ndi kuchotsa machimo athu mu njira yofanana kuti afafanize machimo athu onse.
Anthu onse a Chipangano Chakale, Davide, Abrahamu, ndi ena onse ankadziwa ndi kukhulupirira chimene ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe inkatanthauza kwa iwo. Iyo inavumbulutsa kuti Mesiya, Kristu (Kristu amatanthauza Mpulumutsi), azadza tsiku lina ndi kutsuka machimo ao onse. Iwo anakhulupirira mu chiombolo chao ndipo anapulumutsidwa ndi chikhulupiriro chao.
Lamulo linali mthunzi wa zokoma zirinkudza. Kupereka nsembe chifukwa cha machimo ao tsiku ndi tsiku, chaka ndi chaka, sikukanatipulumutsa ife motheratu. Choncho, Munthu wangwiro komanso wamuyaya, Iye wopanda chirema, Mwana wa God adayenera kudza ku dziko lapansi.
Ndipo Iye ananena kuti Iye adadza kudzachita chifuniro cha Atate Wake monga kwalembedwa m’buku limene linalembedwa za Iye. “Pamenepo ndinati, Taonani, ndafika, kudzachita chifuniro chanu, Mulungu(God). Achotsa choyambacho, kuti akaike chachiwiricho.” Ndife opulumutsidwa ku machimo athu chifukwa chakuti Yesu Kristu anachotsa machimo athu monga kwalembedwa m’Chipangano Chakale, komanso chifukwa chakuti ife timakhulupirira mwa Iye.
Tiyeni tiwerenge Ahebri 10:10. “Ndi chifuniro chimenecho tayeretsedwa mwa chopereka cha thupi la Yesu Khristu, kamodzi, kwatha.” Ndi chifuniro chimeneco tayeretsedwa mwa copereka cha thupi la Yesu Kristu, kamodzi, kwatha. Kodi ife tayeretsedwa kapena ai? ―Ife tayeretsedwa.―
Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? God Atate anatuma Mwana Wake ndi kupereka machimo athu onse pa Iye kudzera mu Ubatizo ndi kumuweruze Iye kamodzi kokha pa Mtanda. Motero, Iye anaombola tonse a ife amene timavutika ndi uchimo. Chinali chifuniro cha God.
Kuti atipulumutse ife, Yesu anadzipereka Yekha kamodzi kokha, kuti ife tiyeretsedwe. Ife tayeretsedwa. Yesu anadzipereka Yekha chifukwa cha machimo athu ndipo Iye anafa m’malo mwa ife kuti ife tisaweruzidwe.
Nsembe ya Chipangano Chakale inkaperekedwa tsiku lililonse chifukwa chakuti machimo onse atsopano ankafunika nsembe ina kuti atsukidwe.
Tanthauzo Lauzimu Pamene Yesu Anasambitsa Mapazi a Petro
Mu Yohane 13 muli nkhani ya Yesu akusambitsa mapazi a Petro. Iye anatsuka mapazi a Petro ndi cholinga chakuti amusonyeze iye kuti Petro adzachimwa m’tsogolo komanso kumuphunzitsa iye kuti Iye adaombolanso kale machimo onse amenewo. Yesu ankadziwa kuti Petro adzachimwanso m’tsogolo, choncho Iye anathira madzi m’nsambidwe ndi kusambotsa mapazi ake.
Petro anayesa kukana, koma Yesu ananena kuti, “Cimene ndicita Ine, sucidziwa tsopano; koma udzadziwa m’tsogolo mwace” (Yohane 13:7). Zomwe zimenezi zikutanthauza ndi zakuti, ‘Iwe udzachimwanso pambuyo pa zimenezi. Iwe udzandikana Ine ndi kuchimwanso pamene ndatsuka machimo ako onse. Iwe udzachimwa ngakhale pambuyo pa Kukwera Kwanga kumwamba. Choncho, ndikusambitsa miyendo yako kuti ndi chenjeze Satana kuti asakuyese iwe chifukwa chakuti ndatenga machimo ako a m’tsogolo.’
Kodi inu mukuganiza kuti Iye anasambitsa miyendo ya Petro kuti atiuze ife kuti tiyenera kulapa tsiku lililonse? Ayi. Ngati ife timayenera kulapa tsiku lililonse kuti tiomboledwe, Yesu sakachotsa machimo anthu onse kamodzi kokha.
Koma Yesu ananena kuti Iye anatiyeretsa ife kamodzi kokha. Ngati ife timayenera kulapa tsiku lililonse, ife tiyeneranso kubwerera mu nthawi ya m’Chipangano Chakale. Nanga kodi ndindani akanakhala wolungama? Kodi ndindani akanaomboledwa motheratu? Ngakhale ife tinakhulupirira mwa God, kodi ndindani akanakhala opanda uchimo?
Kodi ndindani akanayeretsedwa ndi kulapa? Ife timachimwa mosalekeza tsiku lililonse, choncho kodi ife tingapemphe bwanji kuti tchimo lililonse lichotsedwe? Kodi ife tikanakhala bwanji opanda manyazi pamene tikumuvutitsa Iye tsiku lililonse za chiombolo? Ife timakonda kuiwala machimo athu a m’mawa pamene tsiku latha, komanso machimo a kumadzulo mmawa wa wa tsiku lotsatira. Ndi zosatheka kwa ife kulapa motheratu ku machimo athu onse.
Choncho, Yesu anabatizidwa kamodzi ndi kudzipereka Yekha pa Mtanda kamodzi kuti ife tikhale oyeretsedwa kamodzi kokha. Kodi inu mungamvetsetse zimenezi? Ife tinaomboledwa kamodzi kokha ku machimo athu onse. Ife sitiomboledwa nthawi zonse pamene ife talapa.
| Kodi pali uchimo wina winanso umene ife tikuyenera kupereka mapemphero a kulapa? |
| Ayi |
Ife tapulumutsidwa ku machimo athu pokhulupilira kuti Yesu anatenga machimo athu onse, machimo anu, ndi machimo anga.
“Ndipotu wansembe aliyense amaima tsiku ndi tsiku, natumikira, napereka nsembe zomwezi kawirikawiri, zimene sizingathe konse kuchotsa machimo; koma Iye, (m’mene adapereka nsembe imodzi yamuyaya chifukwa cha machimo, anakhala padzanja lamanja la Mulungu(God);—NKJV) kuyambira pomwepo alindirira, kufikira adani ake aikidwa akhale mpando kumapazi ake. Pakuti ndi chipereko chimodzi anawayesera angwiro chikhalire iwo oyeretsedwa. Koma Mzimu Woyeranso atichitira umboni; pakuti adatha kunena, Ichi ndi chipangano ndidzapangana nao, atapita masiku ajawo, anena Ambuye: Ndidzapereka malamulo anga akhale pamtima pao; ndipo pa nzeru zao ndidzawalemba; ndipo machimo ao ndi kusaweruzika kwao sindidzakumbukiranso. Koma pomwe pali chikhululukiro (Kuchotsa) cha machimo palibenso chopereka cha kwa uchimo” (Ahebri 10:11-18).
Kodi zikutanthauza chiyani kuti “Koma pomwe pali chikhululukiro (Kuchotsa) cha machimo”? Mu 10:18, zikutanthauza kuti uchimo paokha, uchimo uliwonse konse, unathetsedwa kwamuyaya, popanda kuchotsera. God wathetsa machimo onse a dziko lapansi. Kodi inu mukukhulupirira zimenezi? “Koma pomwe pali chikhululukiro (Kuchotsa) cha machimo palibenso chopereka cha kwa uchimo.”
Tiyeni tifotokoze mwachidule tsopano motsatiramu. Ngati Yohane Mbatizi akapanda kuika manja ake pa Yesu, mwanjira ina, ngati iye akadapanda kubatiza Yesu, kodi ife tikadaomboledwa? Ife sitikadaomboledwa. Tiyeni tiganizire mobwerera kumbuyo. Ngati Yesu akadapanda kusankha Yohane Mbatizi monga woimirira wa mtundu wonse wa anthu ndi kutenga uchimo wonse kudzera mwa iye, kodi Iye akadatsuka machimo athu onse? Iye sakadatero.
Lamulo la God ndi lolungama. Ndi lokhala wolungama. Iye sakanangonena kuti Iye anali Mpulumutsi wathu, kuti Iye anachotsa machimo athu onse. Iye adayenera kuchotsa machimo athu mwa kuthupi. Kodi ndi chifukwa chiyani Yesu, God, anadza kwa ife m’thupi? Chifukwa chakuti Iye ankadziwa machimo onse a mtundu wa anthu, machimo a mtima komanso a thupi, kuti achotse machimo onse a mtundu wa anthu, Iye, Mwana wa God, adayenera kudza kwa ife m’thupi.
Ngati Yesu Kristu akadapanda kubatizidwa, machimo athu akanatsalira. Ngati Iye adapachikidwa popanda choyamba kutenga machimo athu, imfa Yake ikanakhala yopanda tanthauzo. Iyo sikadakhala ndi chilichonse chochita ndi ife. Yopanda tanthauzo motheratu.
Choncho, pamene Iye anayamba utumiki Wake wapoyera ali ndi zaka 30, Iye anadza kwa Yohane Mbatizi pa Yordano kuti abatizidwe. Utumiki Wake wapoyera unayamba ali ndi zaka 30 ndipo unatha ali ndi zaka 33. Pamene Iye anali ndi zaka 30, Iye anadza kwa Yohane Mbatizi kuti abatizidwe. “Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kuchita choncho kuti anthu onse apulumutsidwe ndi kukhala olungama. Ndi chinthu choyenera kuchita. Tsopano ndibatize Ine.” Inde, Yesu Kristu anabatizidwa ku chiombolo cha anthu onse.
Chifukwa chakuti Yesu anabatizidwa ndi kutenga machimo athu onse, komanso chifukwa chakuti machimo athu onse anaperekedwa pa Iye kudzera mu kuika manja a Yohane Mbatizi, God Mwini anayang’ana kumbali pamene Yesu ankafa pa Mtanda. Ngakhale kuti Yesu anali Mwana Wake wobadwa yekha, Iye adayenera kulola Mwana Wake kuti afe.
God ndi chikondi, koma Iye adayenera kulola Mwana Wake kuti afe. Choncho, kwa maora atatu, kunali m’dima pa dziko lonse. Yesu anafuula asanafe Iye kuti, “Eli, Eli, lama sabakitani? ndiko kunena kuti, Mulungu(God) wanga, Mulungu(God) wanga, mwandisiyiranji Ine?” (Mateyu 27:46). Yesu anasenza machimo athu onse ndi kulandira chiweruzo pa Mtanda chifukwa cha ife. Motero, Iye anatipulumutsa ife. Popanda Ubatizo wa Yesu, imfa Yake ikanakhala yopanda tanthauzo.
| Kodi ndinu ochimwa kapena munthu wolungama? |
| Munthu wolungama amene ndilibe uchimo uliwonse mu mtima mwanga |
Ngati Yesu akadafa pa Mtanda popanda kutenga machimo athu onse, popanda kubatizidwa, imfa Yake sikadakwaniritsa chiombolo. Kuti atiombole ife, Yesu anabatizidwa ndi Yohane, woimirira wa anthu onse, ndi kulandira chiweruzo pa Mtanda kuti iwo onse amene amakhulupilira mwa Iye apulumutsidwe.
Choncho, kuyambira masiku a Yohane Mbatizi kufikira tsopano lino, ufumu wa kumwamba uli wokangamizidwa. Chifukwa chakuti Yohane Mbatizi anasamutsira machimo onse a dziko lapansi pa Yesu, machimo a inu ndi ine anatetezeredwa. Choncho, inu ndi ine tingaitane tsopano God Atate wathu ndipo molimba mtima kulowa mu ufumu wa kumwamba.
Mu Ahebri 10:18, “Koma pomwe pali chikhululukiro (Kuchotsa) cha machimo palibenso chopereka cha kwa uchimo.” Kodi ndinu nonse ochimwa? Tsopano kuti Yesu walipira kale ngogole yanu yonse, kodi inu mukuyenerabe kulipira ngongole?
Kunali munthu amene kuledzera kwake kunamuika iye mu ngongole zambiri. Kenako, tsiku lina, mwana wake adapeza ndalama zambiri ndi kulipira ngongole yonse ya atate wake, komanso kuperekeratu mokwanira ndalama zambiri. Atate wake sakanakhalanso ndi ngongole ngakhale iwo akanamwa momwa wochuluka bwanji.
Izi ndi zomwe Yesu watichitira ife. Iye analipiriratu mokwanira machimo athu onse. Osati machimo okha a moyo wathu wonse, koma machimo onse a dziko lapansi. Iwo onse anaperekedwa pa Yesu pamene Iye anabatizidwa. Choncho kodi ndinu ochimwa tsopano? Ayi, sindinu ochimwa.
Ngati ife tikadadziwa Uthenga Wabwino umenewu wa chiombolo kuyambira pachiyambi, kodi zikakhala zophweka bwanji kwa ife kukhulupirira mwa Yesu. Koma monga zilili, uwo umamveka watsopano kuti athu ambiri amadabwa nawo.
Koma ichi si chinachake chatsopano. Uwo wakhalapo kuchokera pachiyambi. Ife sitinadziwe chabe za uwo m’mbuyomu. Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu Woyera wakhala nthawi zonse wolembedwa m’Malemba ndipo wakhala nthawi zonse wokhala ndi mphamvu. Uwo unalipo nthawi yonseyi. Uwo unali pano inu ndi ine tisanabadwe. Uwo unalipo kuyambira pamene dziko lapansi linalengedwa.
Uthenga Wabwino wa Chiombolo Cha Muyaya
| Kodi ife tiyenera kuchita chiyani pamaso pa God? |
| Ife tiyenera kukhulupilira Uthenga Wabwino wa chiombolo cha muyaya. |
Yesu Kristu, amene anatitsukira machimo athu onse, anachita icho ngakhale inu ndi ine tisanabadwe. Iye anachotsa iwo onse. Kodi inu muli ndi uchimo? ―Ayi.― Ndiye bwanji za machimo amene inu mudzachita mawa? Iwo aphatikidwanso m’machimo a dziko lapansi.
Tiyeni tichotse nkhawa ya machimo a mawa. Machimo amene ife tachita kufikira tsopano anaphatikidwanso m’machimo a dziko lapansi, kodi iwo sanaphatikizidwe? Kodi iwo anaperekedwa pa Yesu kapena ai? Inde, iwo anaperekedwa.
Nanga kodi machimo a mawa anaperekedwanso pa Iye? Inde, Iye anachotsa iwo onse, popanda kuchotsera. Iye sanasiye ngakhale tchimo limodzi m’mbuyo. Uthenga Wabwino umatiuza ife kuti tikhulupirire ndi mtima wonse kuti Yesu anachotsa machimo athu onse, kamodzi kokha, ndi kulipira onse a iwo.
“Chiyambi chake cha Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu(God).” (Marko 1:1) Uthenga Wabwino wa kumwamba ndi nkhani yosalatsa. Iye amatifunsa ife kuti, “Ndinachotsa machimo anu onse. Ndine Mpulumutsi wanu. Kodi inu mumakhulupirira mwa Ine?” Mwa anthu osawerengeka, ochepa okha amayankha kuti, “Inde ndimakhulupirira. Ndimakhulupirira monga Inu mwatiuzira ife. Zinali zophweka kwambiri kuti ndinamvetsetsa nthawi yomweyo.” Iwo amene amanena zimenezi amakhala olungama monga Abrahamu.
Koma ena amanena kuti, “Sindingakhulupirire uwo. Ukumveka watsopano kwambiri komanso wachilendo kwa ine.”
Ndiye Iye amafunsa kuti, “Tangondiuza Ine, kodi ndinachotsa machimo ako onse kapena ai?”
“Ndinaphunzitsidwa kuti Inu munachotsa uchimo woyambilira, koma osati machimo anga a tsiku ndi tsiku.”
“Ndazindikira kuti ndiwe wamzeru kwambiri kukhulupirira zomwe Ndinanena. Popeza Ndiribenso chonena kwa iwe, uyenera kupita ku gahena.”
Ife tapulumutsidwa pokhulupirira mu chiombolo Chake chonse. Iwo onse amene amalimbikira kuti iwo ali ndi uchimo ayenera kupita ku gahena. Ndi chisankho chao chawo.
Uthenga Wabwino wa chiombolo umayamba ndi umboni wa Yohane Mbatizi. Chifukwa chakuti Yesu anatsuka machimo athu onse pobatizidwa ndi Yohane Mbatizi, ife timayeretsedwa pamene takhulupilira.
Mtumwi Paulo analankhula kwambiri za Ubatizo wa Yesu m’Makala ake. Mu Agalatiya 3:27, “Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Khristu mudavala Khristu.” Kubatizidwa kwa Kristu kukutanthauza kuti ife tili mwa Kristu. Pamene Yesu anabatizidwa, machimo athu onse anaperekedwa pa Iye kudzera mwa Yohane Mbatizi, ndipo machimo athu onse anatsukidwa.
Mu 1 Petro 3:21 akuti, “Chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho Ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbumtima chokoma kwa Mulungu(God), mwa kuuka kwa Yesu Khristu.”
Okhawo amene amakhulupilira mu umboni wa Yohane Mbatizi, Ubatizo wa Yesu, komanso mwazi pa Mtanda, ali ndi chisomo cha chiombolo mkati mwao.
Landirani mu mtima mwanu Ubatizo wa Yesu, chifaniziro cha chipulumutso, ndi kupulumutsidwa.
Ulaliki uwu ukupezekanso mu mtundu wa ebook. Dinani pachikuto cha buku pansipa.