(1 Yohane 5:1-12)
“Yense wokhulupirira kuti Yesu ndiye Khristu wabadwa kuchokera kwa Mulungu(God); ndipo yense wakukonda Iye amene anabala akondanso iye amene anabadwa wochokera mwa Iye. Umo tizindikira kuti tikonda ana a Mulungu(God), pamene tikonda Mulungu(God), ndi kuchita malamulo ake. Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu(God), kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa. Pakuti chilichonse chabadwa mwa Mulungu(God) chiligonjetsa dziko lapansi; ndipo ichi ndi chigonjetso tichigonjetsa nacho dziko lapansi, ndicho chikhulupiriro chathu. Koma ndani iye wogonjetsa dziko lapansi, koma iye amene akhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu(God)? Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, ndiye Yesu Khristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi. Ndipo Mzimu Woyera ndiye wakuchita umboni, chifukwa Mzimu Woyera ndiye choonadi. Pakuti pali atatu akuchita umboni, Mzimu Woyera, ndi madzi, ndi mwazi; ndipo iwo atatu ali mmodzi. Ngati tilandira umboni wa anthu, umboni wa Mulungu(God) uposa; chifukwa umboni wa Mulungu(God) ndi uwu, kuti anachita umboni za Mwana wake. Iye amene amkhulupirira Mwana wa Mulungu(God) ali nao umboni mwa iye; iye wosakhulupirira Mulungu(God) anamuyesa Iye wonama; chifukwa sanakhulupirire umboni wa Mulungu(God) anauchita wa Mwana wake. Ndipo uwu ndi umboniwo, kuti Mulungu(God) anatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene uli mwa Mwana wake. Iye wakukhala ndi Mwana ali nao moyo; wosakhala ndi Mwana wa Mulungu(God) alibe moyo.”
| Kodi Yesu adadza mwa chiyani? |
| Madzi, mwazi ndi Mzimu Woyera |
Kodi Yesu adadza mwa madzi? Inde, iye adadza mwa madzi. Iye adadza mwa Ubatizo Wake. Madzi ndi Ubatizo wa Yesu kudzera mwa Yohane Mbatizi pa Mtsinje wa Yordano. Uwo unali Ubatizo wa chiombolo umene Iye anachotsera machimo onse a dziko lapansi.
Kodi Yesu adadza mwa mwazi? Inde, Iye adadza mwa mwazi. Iye anadza m’thupi la munthu ndipo anabatizidwa kuti achotse machimo onse a dziko lapansi, kenako kulipira mphotho ya uchimo pokhetsa mwazi pa Mtanda. Yesu adadza mwa mwazi.
Kodi Yesu adadza mwa Mzimu Woyera? Inde, Iye adadza mwa Mzimu Woyera. Yesu anali God, koma Iye anadza monga Mzimu m’thupi kuti akhale Mpulumutsi wa ochimwa.
Anthu ambiri sakhulupilira kuti Yesu adadza mwa madzi, mwazi, ndi Mzimu Woyera. Ochepa okha amakhulupilira kuti Yesu ndi Mfumudi ya mafumu, God wa milungu. Anthu ambiri amakaikirabe kuti, ‘Kodi Yesu ndi Mwana weniweni wa God kapena Mwana wa Munthu?’ Ndipo ambiri, kuphatikiza azaumilungu komanso otumikira, amakhulupilira mwa Yesu monga munthu osati monga God, Mpulumutsi, komanso Chokhalapo kwathunthu.
Koma God ananena kuti yense amene amakhulupilira kuti Yesu ndi Mfumu ya mafumu onse, God woona, komanso Mpulumutsi weniweni adzabadwa mwa Iye. Iwo amene amakonda God amakonda Yesu, ndipo iwo amene amakhulupiliradi mwa God amakonda Yesu m’njira yofanana.
Munthu sangagonjetse dziko lapansi. Mtumwi Yohane anatiuza ife kuti Akristu oona okha ndi amene angagonjetse dziko lapansi. Chifukwa chimene okhulupirika amagonjetsera dziko lapansi ndi chakuti iwo ali ndi chikhulupiriro m’madzi, mwazi ndi Mzimu Woyera wa Yesu. Mphamvu yogonjetsera dziko lapansi singachokere mu chifuniro cha munthu, kuyesa, kapena kutentheka.
“Ndingakhale ndilankhula malilime a anthu, ndi a angelo, koma ndilibe chikondi, ndikhala mkuwa woomba, kapena nguli yolira. Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndili nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndilibe chikondi, ndili chabe. Ndipo ndingakhale ndipereka chuma changa chonse kudyetsa osauka, ndipo ndingakhale ndipereka thupi langa alitenthe m’moto, koma ndilibe chikondi, sindipindula kanthu ai.” (1 Akorinto 13:1-3) ‘Chikondi’ chomwe chikunenedwa apa chikutanthauza Yesu, amene adadza mwa madzi, mwazi, ndi Mzimu Woyera.
Yekhayo Amene Amakhulupilira mwa Madzi ndi Mwazi Angathe Kugonjetsa Dziko Lapansi
| Kodi ndindani amene angagonjetse dziko lapansi? |
| Iye amene amakhulupilira mu chiombolo cha Ubatizo wa Yesu, cha mwazi Wake ndi cha Mzimu Woyera |
Mu 1 Yohane 5:5-6 akuti, “Koma ndani iye wogonjetsa dziko lapansi, koma iye amene akhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu(God)? Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, ndiye Yesu Khristu.”
Akristu anzanga, Iye amene anagonjetsa dziko lapansi, amene anagonjetsa Satana anali Yesu Kristu. Iye amene amakhulupilira m’mau a madzi, mwazi, ndi Mzimu Woyera wa Yesu adzagonjetsanso dziko lapansi. Kodi Yesu anagonjetsa bwanji dziko lapansi? Kudzera mu chiombolo cha madzi, mwazi, ndi Mzimu Woyera.
Mbaibulo, ‘madzi’ amalozera ku ‘ubatizo wa Yesu’ (1 Petro 3:21). Yesu anadza ku dziko lino lapansi m’thupi. Iye anadza kudzapulutsa ochimwa a dziko lapansi; Iye anabatizidwa kuti achotse machimo a wochimwa onse a dziko lapansi ndipo Iye anafa pa Mtanda kuti atetezere machimo amenewo.
Mwazi pa Mtanda umalozera ku choona chakuti Iye anadza ku dziko lino lapansi m’thupi monga munthu. Iye anadza m’maonekedwe a thupi la munthu kuti apulumutse ochimwa ndipo anabatizidwa ndi madzi. Choncho, Yesu anadza kwa ife mwa zonse madzi ndi mwazi. Mwanjira ina, Iye anachotsa machimo onse a dziko lapansi ndi madzi a ubatizo Wake ndi mwazi wa imfa Wake.
Kodi Satana analamulira bwanji dziko lapansi? Satana anapangitsa mtundu wa anthu kuti akaikire mau a God ndi kudzala mbeu za kusamvera m’mitima mwao. Mwanjira ina, Satana anasandutsa mtundu wa anthu kukhala atumiki ake powanyenga iwo kuti asamvere mau a God.
Komabe, Yesu anadza ku dziko lino lapansi ndi kufafaniza machimo onse a anthu ndi madzi a ubatizo Wake ndi mwazi Wake pa Mtanda: Iye anagonjetsa Satana ndi kufafaniza machimo onse a dziko lapansi.
Zimenezi zinachitika chifukwa chakuti Yesu Kristu anali Mpulumutsi wa ochimwa. Iye anakhala Mpulumutsi wathu chifukwa chakuti Iye anadza mwa madzi ndi mwazi.
Yesu Anachotsa Machimo Onse a Dziko Lapansi ndi Ubatizo Wake wa Chiombolo
| Kodi zikutanthauza chiyani kuti Yesu anagonjetsa dziko lapansi? |
| Zikutanthauza kuti Iye anachotsa machimo onse a dziko lapansi. |
Popeza Yesu anabatizidwa kuti achotse machimo onse a dziko lapansi ndipo anafa kuti awayanjanitse, Iye anakhoza kutipulumutsa ife ku machimo onse. Chifukwa chakuti Yesu anabatizidwa mu Mtsinje wa Yordano ndi Yohane Mbatizi, woimirira wa anthu wonse, machimo onse a dziko lapansi anaperekedwa pa Iye. Ndipo Iye anapereka moyo Wake pa Mtanda kuti alipire mphoto ya uchimo. Chifukwa chakuti Iye anafa ndipo anauka kwa akufa, Iye anagonjetsa mphamvu ya Satana. Iye analipira mphoto ya uchimo ndi imfa Wake.
Yesu Anadza kwa Ochimwa mwa Madzi a Ubatizo ndi Mwazi pa Mtanda
Mtumwi Yohane ananena kuti chiombolo si cha madzi chabe, koma cha madzi ndi cha mwazi. Choncho, monga Yesu adayenera kutenga machimo onse ndi kuchotsa machimo athu kwa muyaya, ochimwa onse anapulumutsidwa ku uchimo pokhulupilira mwa Iye, komanso pokhala okhulupirika ku Mau Wake.
| Kodi Iye anagonjetsa bwanji mphamvu ya Satana? |
| Kudzera mu Ubatizo Wake, mwazi ndi Mzimu Woyera |
Pamene Yesu anadza ku dziko lapansi, Iye anachotsa machimo onse a dziko lapansi. Iye anachotsa machimo athu onse ndi ubatizo Wake mu Yordano ndi kulipira mphotho ya machimo amenewo pa Mtanda; Iye analipira machimo athu ndi imfa Wake. Ndipo uneneri wa lamulo lolungama la God limene limanena kuti ‘mphotho yake ya uchimo ndi imfa’ (Aroma 6:23) unakwaniritsidwa.
Kodi Yesu anatanthauza chiyani pogonjetsa dziko lapansi? Chikhulupiliro chimene chimagonjetsa dziko lapansi ndi chikhulupiliro mu uthenga wabwino wa chiombolo chimene Yesu anatibweretsera ife mwa madzi ndi mwazi. Iye anadza m’maonekedwe a thupi ndipo Iye anachitira umboni za chipulumutso ndi Ubatizo Wake wa madzi ndi imfa Wake pa Mtanda.
Yesu anagonjetsa dziko lapansi, lotchedwa Satana. Ophunzira a mpingo woyambirira anaima chilimwe ngakhale pamaso pa imfa yachifuniro, osagonjera ku Ufumu wa Chiroma kapena ku mayesero aliwonse a dziko lino.
Ichi chinali chifukwa cha chikhulupiriro chao kuti Yesu anadza mwa madzi (Iye anabatizidwa kuti atenge machimo athu onse), ndipo ndi mwazi pa Mtanda (Iye analipira mphotho ya machimo athu onse ndi imfa Wake).
Yesu anadza mwa Mzimu Woyera (Iye anadza m’thupi la munthu), ndipo Iye anachotsa machimo a ochimwa ndi Ubatizo Wake ndi Mwazi Wake pa Mtanda kuti tonse amene tidzaomboledwa tikhoze kugonjetsa dziko lapansi.
Chimenenso Chifaniziro Chake Chikupulumutsani Tsopano, Ndicho Ubatizo, mwa Kuuka kwa Yesu Khristu (1 Petro 3:21)
| Kodi chifaniziro cha chipulumutso ndi chiyani? |
| Ubatizo wa Yesu |
Kwanenedwa mu 1 Petro 3:21 kuti, “Chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho Ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbumtima chokoma kwa Mulungu(God), mwa kuuka kwa Yesu Khristu.” Mtumwi Petro anachitira umboni kuti Yesu anali Mpulumutsi komanso kuti Iye anadza mwa madzi a ubatizo ndi mwazi.
Zotsatira zake, ife tiyenera kukhulupilira mwa Yesu amene anadza mwa madzi ndi mwazi. Ndipo ife tiyenera kudziwa kuti madzi a ubatizo wa Yesu ndi chifaniziro chimene chimatipulumutsa ife. Mtumwi Petro anatiuza ife kuti ‘madzi’ a ubatizo, ‘mwazi’ ndi ‘Mzimu Woyera’ ndi ‘zinthu zofunika kwathunthu’ mu chiombolo.
Palibe wophunzira amene anakhulupilira m’mwazi pa Mtanda popanda ubatizo wa Yesu. Kukhulupilira kokha m’mwazi ndi kutenga theka lokha a chikhulupiliro choona. Chikhulupiliro cha theka kapena chosakwanira chimazimiririka pakapita nthawi. Koma chikhulupiriro cha iwo amene amakhulupirira mu uthenga wabwino wa madzi, mwazi, ndi Mzimu Woyera chidzalimba kwambiri ndi nthawi.
Komabe, mau a uthenga wabwino wa mwazi akungolimba kwambiri ndi kwambiri m’dziko lino masiku ano. Kodi izi zili choncho chifukwa chiyani? Anthu sakudziwa mau a choonadi, chiombolo cha madzi ndi Mzimu Woyera, choncho sangathe kubadwa mwatsopano.
Nthawi ina, mipingo ya kumadzulo idagwera mu zamatsenga. Iwo ankaoneka kuti akuchita bwino kwa kanthawi, koma atumiki a Satana anathandizira kusandutsa chikhulupiliro kukhala chamatsenga.
Matsenga ndi kukhulupilira kuti mdierekezi adzathawa ngati munthu wajambula mtanda pa chidutswa cha pepala kapena mthabwa, ndipo kuti Satana adzathamangitsidwa ngati munthu amakhulupilira m’mwazi wa Yesu. Kudzera mu zimenezi ndi zikhulupiliro zina zamatsenga, Satana ananyenga anthu kukhulupilira kuti iwo adayenera kokha kukhulupilira m’mwazi wa Yesu. Satana amanamizira kuopa mwazi, kunena kuti Yesu anakhetsera ochimwa.
Komabe, Petro ndi ophunzira ena onse anachitira umboni ku uthenga wabwino woona wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi pa Mtanda. Komabe, kodi Akristu masiku ano amachitira umboni ku chiyani? Iwo amachitira umboni ku mwazi okha wa Yesu.
Koma, ife tiyenera kukhulupilira mmau olembedwa m’Baibulo ndi kukhala ndi chikhulupiliro mu chipulumutso cha Mzimu Woyera, cha ubatizo wa Yesu, komanso cha mwazi. Ngati ife tinganyalanyaze Ubatizo wa Yesu ndi kuchitira kokha umboni ku choona chakuti Yesu anafa pa Mtanda chifukwa cha ife, chipulumutso sichingakhale changwiro.
‘Mau a Umboni’ a Chipulumutso cha God
| Kodi ndi umboni wanji kuti God anatipulumutsa ife? |
| Madzi, mwazi, ndi Mzimu Woyera |
Mu 1 Yohane 5:8, ambuye amanena kuti, “Pakuti pali atatu akuchita umboni.” Woyamba ndi Mzimu Woyera, wachiwiri ndi madzi a ubatizo wa Yesu, ndipo wachitatu ndi mwazi pa Mtanda. Zitatu zonse za zinthu zimenezi zili monga chimodzi. Yesu anadza ku dziko lino kudzatipulumutsa ife tonse ku machimo amenewo. Iye yekha anachita zimenezi ndi zonse zitatu, Ubatizo, Mwazi, ndi Mzimu Woyera.
“Pakuti pali atatu akuchita umboni.” Pali zithu zitatu zimene zimatsimikiza kuti God anatipulumutsa ife. Zinthu zitatu zimenezi za umboni ndi madzi a ubatizo wa Yesu, mwazi, ndi Mzimu Woyera. Zinthu zitatu zimenezi ndi zomwe Yesu anatichitira ife m’dziko lino lapansi.
Ngati chimodzi cha zinthu zitatu zimenezi chikanasiyidwa, chipulumutso sichikanakhala chokwanira. Pali atatu akuchita umboni: Mzimu Woyera, madzi, ndi mwazi.
Yesu Kristu amene anadza kwa ife m’thupi ndi God, Mzimu Woyera, komanso Mwana. Iye anadza ku dziko lino lapansi monga Mzimu Woyera m’thupi la munthu ndipo anabatizidwa m’madzi kuti atenge machimo onse a dziko lapansi. Ndipo Iye anatengera machimo onse pa thupi Lake ndi kutipulumutsa ife ochimwa pokhetsa mwazi mpaka imfa pa Mtanda. Iye analipira machimo onse kwathunthu. Ndi uthenga wabwino wa chiombolo chonse mwa madzi, mwazi, ndi Mzimu Woyera.
Ngakhale chimodzi chabe cha zimenezi chikanasiyidwa, kukanakhala kukana chipulumutso cha God chimene chatipulutsa ife ku uchimo onse. Komabe, lero, ambiri a okhulupirira amachitira umboni ndi kukhulupilira kokha mu Uthenga Wabwino wa mwazi ndi Mzimu.
Koma Mtumwi Yohane ananena kuti pali zinthu zitatu zimene zimachita umboni: madzi a ubatizo wa Yesu, mwazi pa Mtanda, komanso Mzimu Woyera. Mtumwi Yohane anali momveka bwino kwambiri mu umboni wake.
Chikhulupiliro chimene chimaombola wochimwa ndi chikhulupiliro mu Mzimu Woyera, madzi, ndi mwazi. Kodi chikhulupiliro chimene chimapanga munthu kugonjetsa dziko lapansi chili kuti? Chili pano. Ndi kukhulupilira mwa Yesu amene anadza mwa madzi, mwazi ndi Mzimu Woyera. Khulupilirani mu zimenezi ndi kulandira chipulumutso ndi moyo wamuyaya.
| Kodi chipulumutso cha God ndi changwiro popanda Ubatizo wa Yesu? |
| Ayi |
Kalekalelo, ndisanabadwe mwatsopano, inenso, ndinali Mkristu amene ndinakhulupilira m’mwazi okha pa Mtanda ndi Mzimu. Ndinakhulupilira kuti Iye anadza monga Mzimu ndi kundifera ine pa Mtanda ndi kundipulumutsa ine ku machimo onse. Ndinakhulupirira kokha mu zinthu ziwiri izi ndipo ndinali wodzikuza mokwanira kufuna kulalikira izo kwa anthu onse.
Ndinakonza kuti ndiphunzire zaumulungu kuti ndikhale m’mishonale kuti ndigwire ntchito ndi kufera anthu monga Yesu anachitira. Ndinakonza zinthu zonse zazikulu.
Koma, malinga ngati ndinakhulupirira mu zinthu ziwiri zokha, munali uchimo wotsalira mu mtima mwanga nthawi zonse. Zotsatira zake, sindinkatha kugonjetsa dziko lapansi. Sindinkatha kukhala womasuka ku uchimo. Pamene ndinakhulupirira kokha m’mwazi ndi Mzimu, ndinali ndidakali ndi uchimo mu mtima mwanga.
Chifukwa chimene ndinali ndidakali ndi uchimo mu mtima mwanga ngakhale ndinakhulupilira mwa Yesu chinali chakuti sindinadziwe za madzi, Ubatizo wa Yesu. Chiombolo changa sichinali chokwanira mpaka ndinaomboledwa pokhulupirira mu madzi a ubatizo, mwazi, ndi Mzimu Woyera.
Chifukwa chimene ndinali olephera kugonjetsa machimo a kuthupi chinali chakuti sindinadziwe tanthauzo la ubatizo wa Yesu. Ngakhale tsopano anthu ambiri amakhulupilira mwa Yesu koma amachitabe machimo a kuthupi. Iwo adakali ndi uchimo m’mitima mwawo ndipo amayesa chilichonse kuti abwezeretse chikondi choyamba chimene anali nacho kwa Yesu.
Iwo sangathe kubwezeretsa kutentheka kwa chidwi chawo choyamba chifukwa sanachapidwepo konse kwathunthu ku machimo awo ndi madzi. Chifukwa chakuti iwo sazindikira kuti machimo awo onse anaperekedwa kwa Yesu pamene Iye anabatizidwa, iwo sangathe kubwezeretsa chikhulupiriro chawo kachiwiri atagwa.
Ndikufuna kupanga izi zimveke bwino kwa inu nonse. Titha kukhala mu chikhulupiriro ndi kugonjetsa dziko lapansi pamene tikhulupirira mwa Yesu. Ngakhale tili osakwanira bwanji, ngakhale timachimwa mochuluka bwanji m’dziko lino, malinga ngati tikhulupirira mwa Yesu ngati Mpulumutsi wathu amene anatipanga ife kukhala omasuka kwathunthu ku uchimo ndi ubatizo Wake, titha kuima mwachigonjetso.
Komabe, ngati ife timakhulupilira mwa Yesu popanda madzi a ubatizo, ife sitingaomboledwe motheratu. Mtumwi Yohane anatiuza ife kuti chikhulupiliro chimene chimagonjetsa dziko lapansi ndi chikhulupiliro mwa Yesu Kristu amene anadza mwa madzi a ubatizo, mwazi ndi Mzimu Woyera.
God anatuma Mwana Wake wobadwa yekha kwa ife kuti aombole iwo amene amakhulupilira mu Ubatizo ndi Mwazi Wake. Yesu anachotsa machimo athu onse ndi ubatizo Wake. Yesu, Mwana yekha wa God, anadza kwa ife mu Mzimu Woyera (m’thupi la munthu). Ndipo Iye anakhetsa mwazi pa Mtanda kuti alipire mphotho ya uchimo. Motero Yesu anapulumutsa anthu onse ku uchimo.
Chikhulupiliro chimene chimatitsogolera ife kuti tigonjetse dziko lapansi chimachokera ku kukhulupilira mu choonadi chakuti Yesu anadza kwa ife mwa madzi, mwazi, ndi Mzimu Woyera ndi kutimasula ife motheratu ku machimo onse.
Pakadapanda kuti pakhale madzi aubatizo ndi mwazi pa Mtanda, sipakanakhala chipulumutso chenicheni. Popanda mmodzi kapena winayo, sitikanakhala ndi chipulumutso chenicheni. Chipulumutso chenicheni sichingakwaniritsidwe popanda madzi ndi mwazi ndi Mzimu Woyera.
Choncho, ife tiyenera kukhulupilira m’madzi, mwazi, ndi Mzimu Woyera. Dziwani zimenezi ndipo inu mudzakhala ndi chikhulupiliro choona.
Ndi Kukuuzani Inu Kuti Si Chipulumutso Choona popanda Umboni wa Madzi, Mwazi, ndi Mzimu Woyera
| Kodi zinthu zitatu zofunika zimene zimachitira umboni ku chipulumutso ndi chiyani? |
| Madzi, mwazi ndi Mzimu Woyera |
Wina angaganizire za funso lili pamwambapa motere: “Yesu ndi Mpulumutsi wanga. Ndimakhulupilira m’mwazi pa Mtanda ndipo ndikufuna kufa monga ofera chikhulupiliro. Ndimakhulupilira mwa Yesu ngakhale ndili ndi uchimo mu mtima mwanga. Ndalapa molimbika komanso kugwira ntchito molimbika kuti ndichite khalidwe labwino, lolungama, komanso la chifundo tsiku lililonse. Ndapereka moyo wanga komanso chuma changa chonse cha dziko kwa Inu. Sindinakwatire nkomwe. Kodi God sangandidziwe ine bwanji? Yesu anandifera ine pa Mtanda. God wathu Woyera anadza monga munthu ndi kutifera ife pa Mtanda. Ndinakhulupilira mwa Inu, kudzipereka chifukwa cha Inu, komanso kuchitira Inu ntchito yanga mokhulupirika. Ngakhale ndingakhale wosayenera ndipo ndidakali ndi uchimo mu mtima mwanga, kodi Yesu adzandipititsa ine ku gahena chifukwa cha zimenezo? Ayi, Iye sadzandipititsa ku gahena.”
Pali anthu ambiri otere. Iwo ndi amene sakhulupilira kuti Yesu anabatizidwa kuti achotse machimo onse a dziko lapansi. Pamene anthu amenewa amene amakhulupilira mwa Yesu adakali ndi uchimo, kodi iwo amapita kuti? Iwo amapita ku gahena. Iwo ndi ochimwa!
Iwo, amene amaganiza monga afunira ndi kudzitengera kuti God ayenera kuganiza chimodzimodzi, adzapita ku gehena. Kuonjezera apo, ena amanena kuti chifukwa chakuti Yesu anachotsa uchimo onse pamene Iye anafa pa Mtanda, mulibe uchimo m’dziko lapansi. Komabe, izi zikukamba kokha za mwazi ndi Mzimu. Ichi si chikhulupiliro chimene chimatsogolera anthu ku chiombolo chonse.
Ife tiyenera kukhulupirira kuti Yesu anachotsa machimo athu ndi ubatizo Wake, anaweruzidwa, ndi kufa pa Mtanda chifukwa cha ife, komanso kuti Iye anauka masiku atatu pambuyo pa imfa Wake.
Popanda chikhulupiriro chotero, chiombolo chathunthu sichikhala chotheka. Yesu Kristu anabatizidwa, kufa pa Mtanda, ndipo anauka. Yesu Kristu anadza kwa ife mwa madzi, mwazi, ndi Mzimu Woyera. Iye anachotsa machimo onse a dziko lapansi.
Pali zinthu zitatu zofunika kwambiri zimene zimachitira umboni: Mzimu Woyera, madzi, ndi mwazi.
Choyamba, Mzimu Woyera amachitira umboni kuti Yesu ndi God komanso kuti Iye anatsika m’thupi la munthu.
Chinthu chachiwiri ndi umboni wa ‘madzi’. Madzi ndi ubatizo wa Yesu mu Yordano kudzera mwa Yohane Mbatizi, umene machimo athu anaperekedwa pa Yesu kudzera mwa uwo. Machimo athu onse anaperekedwa pa Yesu pamene Iye anabatizidwa (Mateyu 3:15).
Mboni yachitatu ndi mwazi umene umaimira moyo watsopano komanso Yesu kuvomera udindo wa chiweruzo cha machimo athu m’malo mwa ife. Yesu anatifera ife ndi kuvomera chiweruzo cha Atate Wake chifukwa cha ife ndipo anaukitsidwa patapita masiku 3.
God Atate amatuma Mzimu Woyera m’mitima ya iwo amene amakhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Mwana Wake kuti uchitire umboni za chiombolo chathu.
Iwo amene abadwa mwatsopano ali ndi Mau amene amagonjetsera dziko lapansi. Owomboledwa adzagonjetsa Satana, bodza la aneneri onyenga, komanso zotchinga, kapena zopanikiza zimene zimadza kwa iwo mosalekeza. Chifukwa chimene ife timakhala ndi mphanvu imeneyi ndi chakuti ife tili ndi zinthu zitatu m’mitima mwathu: madzi a Yesu, mwazi Wake, ndi Mzimu Woyera.
| Kodi ife timagonjetsa bwanji dziko lapansi ndi Satana? |
| Pokhulupilira mu umboni utatu |
Ife timagonjetsa Satana ndi dziko lapansi chifukwa chakuti ife timakhulupilira mu Mzimu Woyera, madzi, ndi mwazi. Iwo amene amakhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu ndi othekera kugonjetsa mtundu uliwonse wa aneneri onyenga. Chikhulupiriro chathu, ndi mphamvu iyi yogonjetsa, chili mu madzi, mwazi, ndi Mzimu Woyera. Kodi inu mukukhulupilira mu zimenezi?
Inu simungabadwe mwatsopano kapena kugonjetsa dziko lapansi ngati inu mulibe chikhulupiriro mu chiombolo kudzera mu ubatizo wa Yesu, mwazi Wake, komanso kukhulupilira kuti Yesu ndi Mwana wa God komanso Mpulumutsi wathu. Kodi zimenezi zili mu mtima mwanu?
Kodi inu muli ndi Mzimu Woyera ndi madzi mu mtima mwanu? Kodi inu mumakhulupilira kuti machimo anu onse anaperekedwa pa Yesu? Kodi inu muli ndi mwazi wa Mtanda mu mtima mwanu?
Inu mudzagonjetsa dziko lapansi ngati muli ndi ubatizo, madzi a Yesu mu mtima mwanu, ndipo ngati mumakhulupirira kuti Yesu anafa pa Mtanda chifukwa cha inu komanso kuti Iye anatenga chiweruzo chifukwa cha inu.
Mtumwi Yohane anagonjetsa dziko lapansi chifukwa chakuti iye anali ndi zinthu zonse zitatu zofunika zimenezi mu mtima mwake. Iye analankhulanso za chiombolo kwa abale ake onse mu chikhulupiriro amene ankapilira zotchinga komanso kuopsezedwa mu ntchito yawo. Iye anachitira umboni kuti, “Umu ndi momwe inunso mungagonjetsere dziko lapansi. Yesu anadza mwa Mzimu Woyera, madzi, ndi mwazi. Monga momwe Iye anagonjetsera dziko lapansi, iwo amene amakhulupirira mu Mzimu Woyera, madzi, ndi mwazi adzagonjetsanso dziko lapansi. Iyi ndi njira yokhayo kwa okhulupirika yogonjetsera dziko lapansi.”
Mu 1 Yohane 5:8, kwanenedwa kuti, “Pakuti pali atatu akuchita umboni, Mzimu Woyera, ndi madzi, ndi mwazi; ndipo iwo atatu ali mmodzi.” Ambiri amakambabe za mwazi ndi Mzimu, koma iwo amasiya madzi a ubatizo wa Yesu. Ngati iwo amasiya ‘madzi’, iwo ndi onyengedwabe ndi Satana. Iwo ayenera kuchoka kumbuyo kwa kudzinyenga kwao ndi kulapa; iwo ayenera kukhulupilira ‘m’madzi’ a Ubatizo wa Yesu, wa kubadwa mwatsopano.
Palibe amene angagonjetse dziko lapansi popanda kukhulupirira m’madzi ndi mwazi. Ndikunenanso kwa inu, palibe! Ife tiyenera kumenya nkhondo pogwiritsa ntchito madzi ndi mwazi wa Yesu monga zida zathu. Mau Wake ndi lupanga la Mzimu Woyera, Kuunika.
Padakali ambiri kwambiri amene sakhulupirira mu Ubatizo wa Yesu umene unatsuka machimo awo onse. Padakali ambiri kwambiri amene amakhulupirira mu zinthu ziwiri zokha. Pamene Yesu awauza kuti ‘Nyamuka, wala’, iwo sangawale. Iwo adakali ndi uchimo mu mtima mwawo. Ngakhale iwo amakhulupirira mwa Yesu iwo amatherabe mu gehena.
Uthenga Wabwino wa Ubatizo ndi Mwazi wa Yesu Uyenera Modziwikiratu Kuchitiridwa Umboni Kuti Anthu Amve, Akhulupilire, ndi Kupulumutsidwa
| Kodi chikhulupiliro mu ubatizo Wake ndi chiphunzitso chabe? |
| Ayi, si chiphunzitso. Ndi choonadi. |
Pamene ife tichitira umboni za uthenga wabwino, ziyenera kukhala zotsimikizika. Yesu anadza mwa Mzimu Woyera, mwa Ubatizo (umene unachotsa machimo athu), komanso mwa mwazi (umene unalipira machimo athu). Ife tiyenera kukhulupilira mu zonse zitatu zimenezi.
Ngati si choncho, ife sitimalalikira uthenga wabwino koma m’malo mwake chipembedzo chophweka. Akristu m’dziko lino lapansi amatchula Chikristu chipembedzo. Chikristu sichingafotokozedwe ngati chipembedzo. Ndi chikhulupiliro cha chiombolo chomangidwa pa choonadi, chikhulupiliro choyang’ana kwa God. Si chipembedzo.
Chipembedzo ndi chinthu chopangidwa ndi munthu, pamene chikhulupiliro ndi kuyang’ana ku chipulumutso chimene God anatipatsa ife. Uko ndiye kusiyana kwake. Ngati inu mumanyalanyaza choonadi ichi, inu mumatenga Chikristu ngati chipembedzo chabe china ndi kulalikira mwa njira ya makhalidwe ndi khalidwe labwino.
Yesu Kristu sanabwere kudzakhazikitsa chipembedzo m’dziko lino lapansi. Iye sanakhazikitsepo chipembedzo chotchedwa Chikristu. Kodi ndi chifukwa chiyani inu mumakhulupirira kuti ndi chipembedzo? Ngati zonse ndi zofanana, kodi ndi chifukwa chiyani osakhulupirira mu Chibuda bwanji? Kodi inu mukuganiza kuti ndikulakwitsa kunena zimenezi?
Anthu ena amakhulupilira mwa Yesu monga chipembedzo ndipo pamapeto pake amanena kuti, “Kodi kusiyana kwake ndi kotani? Kumwamba, Paradiso... Zonse ndi chinthu chimodzi chofanana, izo zili ndi maina chabe osiyana. Ife tonse tikazipeza ku malo ofanana mulimonse.”
Akristu anzanga, ife tiyenera kukumana ndi choonadi. Ndipo ife tiyenera ‘Nyamuka ndi wala.’ Ife tiyenera kunena choonadi popanda kukayika.
Pamene winawake wanena kuti, “Iyo singakhale njira yokhayo”, inu muyenera kunena ndi mau otsimikiza kuti, “Ayi! Ndi njira yokhayo: Inu mungapite kumwamba pokhapo pamene inu mwakhulupirira mwa Yesu Kristu amene anadza mwa madzi, mwazi, ndi Mzimu Woyera.” Inu muyenera kuwala kwambiri kuti miyoyo ina imve mau a chiombolo, kubadwa mwatsopano, ndi kupita kumwamba.
Khalani ndi chikhulupiriro cholondola: Anthu amene sadziwa chiombolo cha ubatizo ndi mwazi wa Yesu ndipo amamukonda Yesu mwa mbali imodzi adzaonongeka
| Kodi ndindani amene adzaonongeka ngakhale iye amakhulupilira mwa Yesu? |
| Iwo amene sakhulupilira mu Ubatizo wa Yesu |
Kunena chabe kuti mumakhulupirira mwa Yesu mwachisawawa ndi chikondi cha mbali imodzi kwa Yesu ndipo chimapanga kutenga choonadi monga chipembedzo chabe.
Sitima imene inkaoloka pa Nyanja ya Pacific inamira ndipo opulumuka ochepa anatsalira pa bwato lamitengo loyandama. Iwo anatumiza bungwe la SOS, koma mafunde aakulu analepheretsa sitima zina kufika kuti ziwathandize iwo. Kenako kunabwera helikopita m’malo mwake ndikuponya chingwe pansi.
Ngati m’modzi wa iwo angagwire chingwecho ndi manja ake m’malo momanga icho mozungulira thupi lake, iye adzakhala ngati munthu wogwera mu chikondi cha mbali imodzi ndi Yesu, kukhulupirira mwa God momwe akufunira. Iye ndi osatetezekabe, koma iye amanena kuti, “Ndimakhulupilira. Ndipulumutseni ine. Ndimakhulupilira, choncho ndikuganiza kuti ndidzapulumutsidwa.”
Iye amene samvetsetsa choonadi cha ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake amakhulupilira kuti adzapulumutsidwa chifukwa chokha chakuti akugwirira chingwe.
Koma pamene iye akukokeredwa m’mwamba, manja ake adzataya mphamvu yogwirira chingwecho. Iye adzakhala akugwirira ndi mphamvu zake zokha. Pamene mphamvu zimenezo zatha, iye adzataya mphamvu yogwirira ndi kugweranso m’nyanja.
Ichi ndi chofanana ndi kukonda Yesu mwa mbali imodzi. Ambiri anganene kuti iwo amakhulupilira mwa God ndi Yesu; kuti iwo amakhulupilira mwa Yesu amene anadza mwa Mzimu Woyera, koma ili ndi gao lokha la choonadi chonse. Iwo kwenikweni sangakhulupilire ngakhalenso kukhala mu uthenga wabwino wangwiro, choncho iwo amadzikakamiza okha kunena mobwereza bwereza kuti iwo amakhulupilira.
Kukhulupilira ndi kuyesa kukhulupilira si chinthu chimodzi. Iwo amanena kuti adzatsatira Yesu mpaka kumapeto koma adzatayidwa pa tsiku lomaliza chifukwa cha tchimo limene limatsalira m’mitima mwawo. Iwo amakonda Yesu popanda kudziwa kuti Yesu anadza mwa ubatizo Wake, mwazi, ndi Mzimu Woyera. Ngati iwo amakonda chifukwa cha mwazi Wake okha, iwo adzapita ku gahena.
Mangani mzimu wanu m’madzi a Ubatizo, ndi mau a mwazi pa Mtanda. Pamene Yesu waponya pansi chingwe cha chipulumutso, iwo amene amadzimanga okha ndi madzi, mwazi, ndi Mzimu Woyera adzapulumutsidwa.
Wopulumutsa wochokera mu helikoputa anafuula kudzera mu chimkuza mau kuti, “Chonde mvetserani mosamala kwa ine. Ndikaponya chingwe pansi, chimangeni mozungulira chifuwa chanu pansi pa mikono yanu. Kenako ingokhalani monga mulili. Musagwire chingwecho ndi manja anu. Ingochimangani mozungulira chifuwa chanu ndi kumasuka. Kenako mudzapulumutsidwa.”
Atatha kupereka malangizo amenewo, munthu mmodzi amene anatsatira malangizowo ndi kudzimanga ndi chingwe anapulumutsidwa. Koma munthu wina ananena kuti, “Osadandaula. Ndine wamphamvu kwambiri. Ndakhala ndikuchita masewera olimbitsa thupi ku malo ochitira masewera. Kodi mungaone minofu yanga? Ndingapachikike kwa makilomita ambiri.” Iye kenako anagwira chingwecho ndi manja ake pamene chingwecho chinakokedwa m’mwamba.
Amuna awiri onse anakokedwera m’mwamba pachiyambi. Koma pali kusiyana. Munthu amene anamvera malangizo ndi kudzimanga yekha chingwe mozungulira anakokedwa popanda vuto. Iye mpaka anakomoka mu njira komabe iye anakokedwa.
Iye amene anadzitama ndi mphamvu zake pamapeto pake analephera kugwira chingwe chifukwa chakuti mphamvu zake zinatha. Ndipo iye anafa chifukwa chakuti iye anakana ndi kunyalanyaza malangizo.
Kuti apeze chiombolo chathunthu, munthu ayenera kukhulupirira mu chiombolo cha madzi a ubatizo Wake ndi mwazi zimene zinapulumutsa miyoyo yonse ku tchimo. Chipulumutso chilipo kwa iwo amene amakhulupirira ndi mtima wonse Mau akuti: “Ndinakupulumutsani inu kwathunthu ndi ubatizo Wanga kudzera mwa Yohane Mbatizi komanso pokhetsera mwazi mpaka kufa pa Mtanda.”
Iwo amene amakhulupilira m’mwazi okha amanena kuti, “Osadandaula, ndimakhulupilira. Ndidzakhala othokoza mpaka kumapeto kwa moyo wanga chifukwa cha mwazi wa Yesu. Ndidzatsatira Yesu mpaka kumapeto ndipo chikhulupiliro changa m’mwazi okha chidzakhala chokwanira kugonjetsa dziko lapansi komanso machimo onse kwa moyo wanga wonse.”
Komabe, izi si zokwanira. Anthu amene God amachitira umboni monga anthu Ake ndi iwo amene amakhulupilira mu zinthu zonse zitatu: kuti Yesu anadza mwa Mzimu Woyera ndipo anabatizidwa (Yesu anachotsa machimo onse ndi ubatizo Wake mu Yordano), kuti Iye anafa pa Mtanda kuti alipire mphotho ya machimo onse, komanso kuti Iye anauka kwa akufa.
Mzimu Woyera amabwera kokha kwa iwo amene amakhulupirira zinthu zonse zitatu izi ndipo amachitira umboni za izo. “Inde, Ndine Mpulumutsi wanu. Ndinakupulumutsani inu ndi madzi ndi mwazi. Ndine God wanu.”
Koma kwa iwo amene sakhulupilira mu zitatu, God sapereka chipulumutso. Ngakhale kuti chimodzi chasiyidwa, God amanena kuti, “Ayi, iwe sunapulumutsidwe.” Ophunzira Wake onse anakhulupilira mu zonse zitatu. Yesu akunena kuti Ubatizo Wake ndi umboni wa chipulumutso, komanso kuti mwazi Wake ndi chiweruzo.
Mtumwi Paulo ndi Petro Anachitiranso Umboni za Ubatizo ndi Mwazi wa Yesu
| Kodi ophunzira a Yesu anachitira umboni za chiyani? |
| Ubatizo wa Yesu ndi Mwazi Wake |
Kodi Mtumwi Paulo analankhulapo za Ubatizo wa Yesu? Tiyeni tione kuti ndi kangati pamene iye anakalankhula za ubatizo wa Yesu. Iye ananena mu Aroma 6:3 kuti, “Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwa Khristu Yesu; tinabatizidwa mu imfa yake?” Komanso pa 6:5 akuti, “Pakuti ngati ife tinakhala olumikizidwa ndi Iye m’chifanizidwe cha imfa yake, koteronso tidzakhala m’chifanizidwe cha kuuka kwake.”
Iye ananenanso mu Agalatiya 3:27 kuti, “Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Khristu mudavala Khristu.” Atumwi a Yesu anachitira umboni za madzi, ubatizo wa Yesu. “Chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho ubatizo.” (1 Petro 3:21).
Chipulumutso cha Chiombolo cha Ambuye Chinadza mwa Madzi ndi Mwazi wa Yesu
| Kodi God amatcha ndani olungama? |
| Iwo amene alibe uchimo uliwonse m’mitima mwao |
Chiombolo chimene Yesu anapereka pa munthu ndi cha madzi a ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda. Mwa chiombolo chimenecho ife tiyenera Nyamuka ndi wala. Motani? Pochitira umboni za zinthu zitatu zimenezi.
“Nyamuka, wala, pakuti kuunika kwako kwafika, ndi ulemerero wa Yehova wakutulukira.” (Yesaya 60:1) God waunika kuwala pa ife ndi kutiuza ife kuti tiwalenso. Ife tiyenera kumvera lamulo limenelo.
Ife tiyenera kulalikira uthenga wabwino ndi mphamvu zonse. Komabe, anthu ambiri, samvera. Khulupilirani mwa Yesu ndipo inu mudzapulumutsidwa. Inu mudzakhala olungama. Ngati mudakali uchimo mu mtima mwanu, sindinu wolungama. Inu simunagonjetsebe machimo a dziko lapansi.
Inu simungathe konse kuchotsa uchimo mu mtima mwanu ngati simukhulupirira m’madzi a Yesu (Ubatizo wa Yesu). Inu simungathe konse kupewe chiweruzo ngati simukhulupirira m’mwazi wa Yesu. Inu simungapulumutsidwe konse ngati inu simukhulupilira mwa Yesu Kristu amene anadza mwa Mzimu Woyera. Simungakhale olungama konse kwathunthu pokhapokha mutakhulupilira maumboni atatu.
Chilungamo chosakwanira chimatsogolera kokha ku ‘chilungamo chotchedwa chotero’. Ngati wina anganene kuti iye adakali ndi uchimo koma kudziyesa yekha munthu wolungama, iye sanakhale mwa Yesu. Anthu ena masiku ano amayesa kupachika chiombolo pa ‘chilungamo chotchedwa chotero’. Iwo alemba zambiri zopanda pake pa phunziro limeneli.
Kodi God amatcha munthu wopanda uchimo pamene muli uchimo mu mtima mwake? Iye sachita choncho. Iye amatcha monga momwe Iye akuonera. Iye ndi wamphamvuyonse koma Iye konse sanganame. Anthu samvetsetsa tanthauzo lenileni la chilungamo. Ife timatcha chinthu kuti ndi ‘choyera’ pokhapo pamene icho ndi choyera. Ife sitimanena kuti ndi ‘choyera’ pamene pali uchimo.
Mutha kuganiza kuti mumazindikiridwa kuti ndinu olungama ndi Yesu ngakhale muli ndi uchimo mumtima mwanu. Zimenezo n’zolakwika.
Yesu amangonenera ife olungama pamene ife takhulupilira mwa Yesu monga Munthu amene anadza mwa Mzimu Woyera, Munthu amene anadza mwa madzi (kuti Iye anachotsa machimo athu onse pamene Iye anabatizidwa), komanso Munthu amene anadza mwa mwazi (Iye anadza m’thupi ndi kufa chifukwa cha ife).
Abale ndi alongo Akristu, ‘chilungamo chotchedwa chotero’ chilibe chochita ndi uthenga wabwino wa madzi ndi mwazi. ‘Otchedwa’, kapena ‘kutchedwa olungama’ ndi chiphunzitso chobadwa ndi anthu. Kodi God amakutchani inu olungama pamene muli ndi uchimo mu mtima mwanu? God samatchula munthu wolungama pamene ali ndi uchimo mu mtima mwake, ngakhale kuti amakhulupirira modzipereka mwa Yesu. Yesu sangathe konse kunama.
Komabe, kodi inu mukuganizabe kuti God amatcha winawake kuti ndi wolungama pamene muli uchimo mu mtima mwake? Izo ndi zimene anthu amaganiza, osati God. God amadana ndi bodza. Kodi Iye angatche inu kuti ndi wolungama pamene inu mumakhulupilira kokha mu ‘Mzimu’ ndi ‘mwazi’? Konse ayi.
Pali mtundu umodzi wokha wa munthu umene God amazindikira kuti ndi wolungama. Ndi munthu amene alibe uchimo uliwonse mu mtima mwake. Iye amazindikira kokha iwo amene amakhulupilira mu zinthu zonse zitatu: kuti Yesu, amene ndi God, anadza ku dziko lapansi m’thupi, kuti Iye anabatizidwa mu Yordano, komanso kuti Iye anakhetsa mwazi pa Mtanda kuti afafanize machimo athu onse.
Okhawo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino wa chiombolo amazindikiridwa ndi God. Iwo ndi amene amakhulupilira molondola. Iwo amakhulupilira motheratu mu zinthu zonse zimene Iye anatichitira ife. Iwo amakhulupilira kuti Yesu anadza ndipo anabatizidwa kuti achotse machimo ao onse komanso kuti Iye anatenga chiweruzo chathu pokufa pa Mtanda, ndipo anauka kwa akufa.
Zinthu zonse zimenezi zinachitika chifukwa cha chikondi cha God. Yesu anadza kuchokera kumwamba ndi kunena kuti, “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.” (Mateyu 11:28) Iye anachita izi potenga machimo athu.
God sazindikira iwo amene amakhulupilira kokha m’mwazi wa Yesu. Iwo amene amakhulupilira kokha m’mwazi wa Yesu adakali ndi uchimo m’mitima mwao.
Kodi Yesu amazindikira ndani monga olungama? “Ndinachotsa machimo anu onse pamene Ndinadza ku dziko lino lapansi ndipo Ndinabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Ndikuchitira umboni kuti machimo onse m’dziko lapansi anaperekedwa pa Ine. Ndinalipilira machimo amenewa pa Mtanda. Ndinakupulumutsani inu motero.” Khulupilirani mu ubatizo wa Yesu, mwazi Wake, komanso choona chakuti Iye ndi God. Zonse ndi zofunika ku chipulumutso.
Kwa iwo amene amakhulupilira mu zitatu zonse, Yesu amanena kuti, “Inde, inu mwapulumutsidwa. Ndinu wolungama komanso ana a God.” Inu mwapulumutsidwa ngati inu mumakhulupilira mu Ubatizo wa Yesu, mwazi Wake, komanso Mzimu Woyera zonse pamodzi. Iwo amene amakhulupilira kokha m’mwazi ndi Mzimu adakali ndi uchimo m’mitima mwao.
Mu ufumu wa God, muli choonadi chimodzi chokha. Pali chilungamo, kuona mtima, chikondi, komanso kukoma mtima. Palibe kachidutswa kakang’ono ka bodza. Mabodza ndi machenjera mulibe kumwamba.
| Kodi ndani amene ‘akucita kusayeruzika’? |
| Munthu amene sakhulupilira mu Ubatizo wa Yesu |
“Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenere mau m’dzina lanu, ndi m’dzina lanunso kutulutsa ziwanda, ndi kuchita m’dzina lanunso zamphamvu zambiri?” (Mateyu 7:22)
God sazindikira konse ntchito izo za munthu. “Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziweni inu nthawi zonse; chokani kwa Ine, inu akuchita kusaweruzika.” (Mateyu 7:23)
“Ndinapereka nyumba ziwiri kwa Inu. Ndinapereka moyo wanga kwa Inu. Kodi Inu simunandione ine? Sindinakukanenipo Inu mpaka mpweya wanga wotsiriza. Kodi inu simunandione ine?”
“Choncho iwe kodi uli ndi uchimo mu mtima mwako?”
“Inde, Ambuye. Ndili nao wochepa.”
“Ndiye choka nao. Palibe wochimwa amene amaloledwa kudza muno.”
“Koma ndinafera chikhulupiliro!”
“Kodi mukutanthauza chiani kuti, ‘munafera chikhulupiliro’? Munangofa kokha chifukwa cha kuuma mtima kwanu. Kodi inu munazindikira ubatizo Wanga ndi mwazi? Kodi Ndinachitira umboni kuti ndinu anthu Anga? Kodi Ndinachitira umboni mu mtima mwanu kuti ndinu anthu Anga? Inu simukhulupilira mu ubatizo Wanga ndipo Ine sindinachitirepo umboni kuti ndinu anthu Anga, komabe inu munamamatira ku chikhulupiliro chanu ndi kufera icho. Kodi ndi liti pamene ndinachitirapo umboni za inu? Inu munachibweretsa nokha. Inu munakonda komanso kuyesa nokha ku chipulumutso chanu. Kodi mukumvetsetsa? Tsopano, chokani.”
Yesu anatiuza ife kuti Nyamuka ndi wala. Anthu owomboledwa amachita mantha pamaso pa Akristu achinyengo ambiri ndi aneneri onyenga ambiri, ndipo amalephera kuwala kwambiri! Koma malawi aang’ono akhoza kuyambitsa moto waukulu. Ngati wina waima molimba mtima ndi kuchitira umboni, dziko lonse lidzawala.
Mu Yesaya 60:1-2, akunena kuti, “Nyamuka, wala, pakuti kuunika kwako kwafika, ndi ulemerero wa Yehova wakutulukira. Pakuti taona, mdima udzaphimba dziko lapansi, ndi mdima wa bii mitundu ya anthu; koma Yehova adzakutulukira ndi ulemerero wake udzaoneka pa iwe.”
Ikutilamula ife kuti nyamuka ndi wala chifukwa chakuti mdima wopanda choonadi komanso uthenga wabwino wonyenga udzakutira dziko lapansi. Okhawo amene amakhulupilira mwa Yesu angathe kukonda Iye. Iwo amene sanaomboledwe sangathe konse kukonda Yesu. Kodi iwo angatero bwanji? Iwo angoyankhula kokha za chikondi koma sangamukondedi Iye pokhapokha ngati iwo akhulupilira.
Pali Zinthu Zitatu Zimene Zimachitira Umboni ku Chipulumutso cha Ochimwa
| Kodi umboni wa chipulumutso mu mtima mwathu ndi chiyani? |
| Ubatizo wa Yesu |
“Pakuti pali atatu akuchita umboni, Mzimu, ndi madzi, ndi mwazi; ndipo iwo atatu ali mmodzi.” Yesu anadza ku dziko lapansi ndipo Iye anachita ntchito Wake ndi madzi ndi mwazi. Iye anachita zimenezi ndipo anatipulumutsa.
“Ngati tilandira umboni wa anthu, umboni wa Mulungu(God) uposa; chifukwa umboni wa Mulungu(God) ndi uwu, kuti anachita umboni za Mwana wake. Iye amene amkhulupirira Mwana wa Mulungu(God) ali nao umboni mwa iye; iye wosakhulupirira Mulungu(God) anamuyesa Iye wonama; chifukwa sanakhulupirire umboni wa Mulungu(God) anauchita wa Mwana wake. Ndipo uwu ndi umboniwo, kuti Mulungu(God) anatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene uli mwa Mwana wake. Iye wakukhala ndi Mwana ali nao moyo; wosakhala ndi Mwana wa Mulungu(God) alibe moyo.” (1 Yohane 5:9-12)
Obadwa mwatsopano amalandira umboni wa anthu. Ife timazindikiridwa monga olungama. Pamene obadwa mwatsopano amene ndi owomboledwa alankhula za choonadi zokhudza chiombolo, anthu sangatsutse icho. Iwo amavomera icho. Iwo amanena kuti ife timakhulupilira molondola, kuti ndife olondola mu chikhulupiliro chathu. Ngati ife tauza iwo momwe ife tinabadwira mwatsopano, palibe amene amatsutsa choonadi cha icho. Amati tikulondola. Ife timalandira umboni wa anthu.
Koma ndime imeneyi amanenanso kuti, “Umboni wa Mulungu(God) uposa; chifukwa umboni wa Mulungu(God) ndi uwu.” Iyo ikunena kuti umboni wa God ndi wa Mwana Wake. Sichoncho? Kodi umboni wa Mwana Wake ndi chiyani? Umboni wakuti God anatipulumutsa ife ndi wakuti Yesu anadza mwa Mzimu Woyera, Iye anadza mwa madzi a chiombolo, komanso kuti Iye anadza mwa mwazi pa Mtanda. Ndipo God amachitira umboni kuti iyi ndi njira yomwe Iye anatipulumutsira ife, komanso kuti ndife anthu Wake chifukwa chakuti ife timakhulupilira.
“Iye amene amkhulupirira Mwana wa Mulungu(God) ali nao umboni mwa iye; iye wosakhulupirira Mulungu(God) anamuyesa Iye wonama; chifukwa sanakhulupirire umboni wa Mulungu(God) anauchita wa Mwana wake.”
Ndime imeneyi ikutiuza ife kwenikweni amene taomboledwa. Iyo ikunena kuti iye amene amakhulupilira mwa Mwana wa God ali ndi umboni mwa iye. Kodi inu muli ndi umboni mu mtima mwanu? Uli mwa inu komanso uli mwa ine. Yesu anadza ku dziko chifukwa cha ife. (Iye anabwera mu thupi kudzera mu thupi la Mariya mwa Mzimu Woyera.) Pamene Iye anali ndi zaka 30, Iye anabatizidwa kuti atenge machimo athu onse pa Iye Mwini. Ndipo ndi machimo athu onse, Iye anaweruzidwa pa Mtanda. Iye anaukitsidwa patatha masiku atatu kuti atipatse ife moyo wosatha. Yesu anatipulumutsa ife motero.
Kodi chikanachitika ndi chiyani kukanakhala kuti Iye sanaukitsidwe? Kodi Iye akanachitira bwanji umboni za ine mmanda? Icho ndi chifukwa chake Iye ndi Mpulumutsi wanga. Izi ndi zomwe ife timakhulupilira.
Ndipo monga momwe Iye ananenera, Iye anatipulumutsa ife ndi ubatizo Wake ndi mwazi. Ndipo chifukwa chakuti ife timakhulupilira, inu ndi ine ndife opulumutsidwa. Umboni uli mwa ine komanso uli mwa inu. Owomboledwa sanyalanyaza konse madzi a ‘ubatizo’ Wake. Ife sitimasiya konse zinthu zimene Iye anachita kuti atipulumutse ife.
“Pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero.” (Mateyu 3:15) Ife sitimakana konse kuti Yesu anachotsa machimo athu onse pa Yordano pamene Iye anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Owomboledwa sangakane konse ‘madzi,’ ubatizo wa Yesu.
Iwo Amene Amakhulupilira koma Ndi Osaomboledwa Amakana mpaka kumapeto Ubatizo wa Yesu
| Kodi ndindani amapanga God kukhala wabodza? |
| Iye amene sakhulupilira mu ubatizo wa Yesu |
Kodi iye anali olondola bwanji pamene Mtumwi Yohane ananena kuti, “Iye wosakhulupirira Mulungu(God) anamuyesa Iye wonama.” Ngati Mtumwi Yohane akanakhala moyo tsopano, kodi iye akanatiuza ife chiyani, Akristu? Iye akanafunsa ngati ‘Yesu anachotsa machimo athu onse pamene Iye anabatizidwa.’
Kodi Yohane Mbatizi sakanachitiranso umboni ku uthenga wabwino kuti Yesu anatiombola ife ndi ubatizo Wake? “Kodi machimo anu sanaperekedwe pa mutu wa Yesu ndipo kodi Iye sananyamule machimo anu pamene Iye anabatizidwa ndi ine?” Iye akanachitira umboni kuti “Yesu anabatizidwa kuti akupulumutseni inu.”
Iwo amene sakhulupilira mwa God, amene sakhulupilira mu zonse zomwe Iye anachita kuti atipulumutse ife, amapanga Iye kukhala wabodza. Pamene ife tanena kuti Yesu anachotsa machimo athu onse pamene Iye anabatizidwa, iwo amanena kuti, “Oh, okondedwa ine! Iye sanatenge machimo athu onse! Iye anachotsa kokha uchimo woyambirira, choncho machimo athu onse atsiku ndi tsiku amatsalabe.”
Iwo amalimbikira kuti iwo ayenera ‘kulapa tsiku lililonse ndi kuvomereza machimo onse atsopano kuti aomboledwe’. Izi ndi zomwe iwo amakhulupilira. Kodi inu nonse mumanenanso zimenezo? Iwo amene sakhulupilira kuti machimo athu anatsukidwa ndi ubatizo wa Yesu akupanga God kukhala wonama.
Yesu Anatiombola Ife Kamodzi Kokha Pamene Iye Anabatizidwa ndi Kukhetsa Mwazi pa Mtanda
| Kodi ndindani akunama? |
| Munthu amene sakhulupilira mu ubatizo wa Yesu |
Yesu anabatizidwa ndi kuchotsa machimo onse kamodzi kokha. God amapulutsa iwo amene amakhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu, koma amakana iwo amene sakhulupilira. Iwo amapita ku gahena. Choncho, kaya ndife opulumutsidwa kapena ai zimatengera pa zimene ife timakhulupilira. Yesu anatiombola ife ku machimo onse a dziko lapansi. Iwo amene amakhulupilira adzapulumutsidwa, ndipo iwo amene sakhulupilira sadzapulumutsidwa chifukwa chakuti iwo apanga God kukhala wabodza.
Anthu sapita ku gahena chifukwa cha zofooka zao, koma chifukwa chakuti iwo sakhulupilira. “Iye wosakhulupirira Mulungu(God) anamuyesa Iye wonama.” (1 Yohane 5:10) Iwo amene sakhulupilira kuti machimo ao onse anaperekedwa pa Yesu adakali ndi uchimo m’mitima mwao. Iwo sanganene kuti iwo alibe uchimo.
Nthawi ina ndinakumanapo ndi mkulu wa mpingo ndi kumufunsa kuti, “Mkulu kodi machimo anga adzachoka ndikakhulupilira mwa Yesu?”
“Kumene iwo adzachoka.”
“Nanga, popeza Yesu anatenga machimo onse a dziko lapansi ndi kunena kuti kunatha, inu mwapulumutsidwa. Sichoncho kodi?”
“Inde, ndapulumutsidwa.”
“Ndiye inu muyenera kukhala opanda uchimo.”
“Inde, ndilibe.”
“Kodi chimachitika ndi chiyani ngati inu mwachimwanso?”
“Ndife anthu chabe. Kodi ife sitingachimwenso bwanji? Choncho ife tiyenera kulapa ndi kutsuka machimo athu tsiku lililonse.”
Mkulu wa mpingo ameneyu adakali ndi uchimo mu mtima mwake chifukwa chakuti iye sadziwa choonadi chonse cha chiombolo.
Anthu onga iye ndi amene akuchitira chipongwe God ndi kumupanga Iye kukhala wabodza. Kodi Yesu, amene ndi God, analephera kuchotsa machimo onse a dziko lapansi? Ndichinthu chokwiyitsa kwambiri. Ngati Yesu sadachotse machimo onse, kodi Iye akanakhala bwanji God wa chipulumutso? Kodi Iye akanatiuza bwanji ife kuti timukhulupilire Iye? Kodi mukufuna kumpanga Iye kukhala wabodza? Ndikupangira kuti musachite zimenezo!
Baibulo limatiuza ife kuti tisamunyoze Iye. Izi zikutanthauza kuti tisamupange Iye kukhala wabodza ndipo tisakayese kumunyenga Iye. Iye sali ngati ife.
Mtumwi Yohane amatiuza ife ndendende za uthenga wabwino wa chiombolo. Anthu ambiri safuna kukhulupilira mu zinthu zimene God anatichitira ife (choona chakuti Yesu Kristu anadza mwa madzi, mwazi, ndi Mzimu Woyera).
Ngati pali iwo amene sakhulupilira monga momwe iwo anauzidwira komanso iwo amene amakhulupilira mu zinthu zimene God watichitira ife (iwo amene amanena pamaso pa God kuti, “Ndine wolungama” komanso ena amene amanena kuti, “Ndine wochimwa”), kodi ndi ati amene akunena zoona?
Iwo amene sakhulupilira mu zinthu zimene God anachita, umboni wa madzi, mwazi, ndi Mzimu Woyera akunama. Iwo ali ndi chikhulupiliro chabodza. Iwo amene sakhulupilira akupanga God kukhala wabodza.
Osamupanga Iye kukhala wabodza. Yesu anadza ku Mtsinje wa Yordano ndipo motero (pobatizidwa) anakwaniritsa chilungamo chonse (kuchotsa machimo a dziko lapansi).
Mzimu Wabodza Umakana Ubatizo wa Yesu komanso Chiyero Wake
| Kodi Satana ndi mdierekezi amakana chiyani? |
| Ubatizo wa Yesu komanso Chiyero Wake |
Iye amene amakhulupilira mwa Mwana Wake ali ndi umboni mwa iye. Munthu owomboledwa amakhulupilira kuti machimo ao anaperekedwa pa Yesu pamene Iye anabatizidwa, komanso kuti iwo anapulumutsidwa ndi madzi ndi mwazi wa Yesu. Iwo amakhulupilira kuti Yesu anabadwa m’dziko lino lapansi kudzera m’thupi la Mariya; Iye anabatizidwa mu Yordano asanafe Iye pa Mtanda; Iye anafa ndipo anaukitsidwa.
Wolungama ali ndi umboni. Umboni wa chipulumutso chathu uli mu chikhulupiliro chathu mwa Yesu, amene anadza mwa madzi, mwazi, ndi Mzimu Woyera. Umboni uli mwa inu. ‘Khalani ndi umboni mwa inu.’ Ndikukuuzani inu: Si chipulumutso ngati palibe umboni; umboni wa chipulumutso uli mwa inu.
Mtumwi Yohane ananena kuti, “Iye amene amkhulupirira Mwana wa Mulungu(God) ali nao umboni mwa iye.” (1 Yohane 5:10) Kodi kukhala ndi umboni ndi kukhulupilira m’mwazi okha pa Mtanda? Kukhulupilira m’madzi koma osati mwazi? Inu muyenera kukhulupilira mu zitatu zonse kuti muzindikiridwe ndi God.
Pokhapo ndi pamene Yesu adzachitira umboni za inu kuti ‘ndinu opulumutsidwa’. Kodi inu mukunena kuti inu mudzakhala ndi umboni ngati inu mumakhulupilira kokha mu ziwiri (mwazi, ndi Mzimu)? Uko kukhala kukhulupilira mwa God m’njira yanu. Uko kukhala ‘kuchitira umboni za inu nokha.’
Pali anthu ambiri otere ndithu. Pali ambiri m’dziko lapansi amene amakhulupilira kokha mu ziwiri mwa zitatu. Iwo amachitira umboni kuti apulumutsidwa ndipo amalemba mabuku za izo. Amayankhula bwino kwambiri! Ndi zokhumudwitsa kwambiri. Iwo amadzitcha okha ‘Alaliki’. Iwo amadzimva kuti si ‘Alaliki okha’, koma ‘achipembedzo’. Iwo sakhulupilira mu ‘madzi’ komabe amadzitamandira za chipulumutso! Amamveka anzeru bwanji! Koma alibe umboni wa God. Ndi maganizo chabe.
Kodi inu mungatche bwanji icho chipulumutso? Okhawo amene amakhulupilira mwa Yesu, amene anadza mwa Mzimu Woyera, madzi, ndi mwazi, ali ndi umboni wa God ndi wa anthu.
Mtumwi Paulo ananena kuti, “Kuti Uthenga Wabwino wathu sunadze kwa inu m’mau mokha, komanso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m’kuchuluka kwakukulu” (1 Atesalonika 1:5). Satana amasangalala pamene anthu amakhulupilira kokha m’mwazi wa Yesu. “Oh, zitsiru inu, inu mwanyengedwa ndi ine... ha-ha!” Pali ambiri amene amakhulupilira kuti pamene anthu akutamanda mwazi wa Yesu, Satana amachoka. Iwo amaganiza kuti Satana ndi wamantha ndi Mtanda. Satana amangotiseweretsa. Ife sitiyenera kupusitsidwa ndi izo.
Pamene chiwanda chalowa mwa munthu, iye akhoza kukhala wopenga ndi kutuluka thovu kukamwa. Si ntchito yovuta kwa mdierekezi. Mdierekezi ali ndi mphamvu zopanga munthu kuchita pafupifupi chilichonse. Mdierekezi amangofunika kugwiritsa ntchito ubongo wake pang’ono. God anampatsa mdierekezi mitundu yonse ya mphamvu kupatula mphamvu ya kupha. Mdierekezi akhoza kupanga munthu kugwedezeka monga tsamba, kukuwa, ndi kutuluka thovu kukamwa.
Pamene zimenezi zachitika, okhulupirira amafuula kuti, “Choka mu dzina la Yesu! Choka!” Ndipo pamene munthuyo watsitsimuka ndi kubwerera ku umunthu wake, iwo amanena kuti unali mwazi wa Yesu umene unali ndi mphamvu. Koma imeneyi si mphamvu ya mwazi Wake. Ndi satana chabe amene ‘amatiseweretsa’.
Satana ndi mdierekezi amaopa kwambiri iwo amene amakhulupilira mwa Yesu, amene watitsuka ife moyera ndi ubatizo Wake, komanso amene anatenga chiweruzo chifukwa cha ife ndi mwazi Wake, ndipo pa tsiku lachitatu anaukitsidwa. Satana sadzakhala mozungulira mboni ya ubatizo wa Yesu ndi chipulumutso cha mwazi.
Monga momwe inu mukudziwa, ansembe Achikatolika nthawi zina amaturutsa Satana. Ife taona izo m’makanema. Mukanema wotchedwa ‘The Omen,’ wansembe ananyamula mtanda wamatabwa ndi kugwedeza uwo koma wansembeyo anafa. Munthu amene anabadwa mwatsopano sakanagonjetsedwa motere.
Iye amalankhula molimba mtima za madzi ndi mwazi wa Yesu. Pamene mdierekezi wayesa kumuzunza iye, iye angafunse mdierekezi kuti, “Kodi iwe ukudziwa kuti Yesu anachotsa machimo anga onse?” Mdierekezi adzathawa pamenepo. Mdierekezi amadana kukhala pafupi ndi ‘obadwa mwatsopano’. Ngati ‘wobadwa mwatsopano’ wangokhalako, mdierekezi adzayesa kuthawa. Kwanenedwa kuti iwo amene sakhulupilira mwa God amamupanga iye kukhala wabodza. Iwo sakhulupilira mu umboni wa Mwana Wake, umboni wa madzi ndi mwazi.
| Kodi umboni wa Mwana wa God ndi chiyani? |
| Ubatizo Wake, mwazi Wake, ndi Mzimu Woyera |
Kodi umboni wa Mwana wa God ndi chiyani? Ndi wakuti Iye anadza mwa Mzimu Woyera ndi kuchotsa machimo athu ndi madzi. Iye anatenga machimo onse a dziko lapansi pa Iye Mwini ndipo Iye anakhetsa mwazi pa Mtanda chifukwa cha ife. Kodi icho si chiombolo cha madzi, mwazi, ndi Mzimu Woyera?
Anthu amanena bodza pamaso pa God chifukwa chakuti iwo sakhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi mwazi, uthenga wabwino wa chiombolo. Zikhulupiliro zao ndi zabodza, ndipo iwo amafalitsa mabodza amenewa.
Tiyeni titembenukire ku 1 Yohane 5. Ndime ya 11 ikunena kuti, “Ndipo uwu ndi umboniwo, kuti Mulungu(God) anatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene uli mwa Mwana wake.” Iyo ikutiuza ife kuti God watipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo uli mwa munthu amene walandira uyo. Komanso, moyo umenewu uli mwa Mwana Wake.
Iwo amene amalandira moyo wosatha ndi iwo amene aomboledwa pokhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Owomboledwa amalandira moyo wosatha ndi kukhala kwamuyaya. Kodi inu mwalandira moyo wosatha?
Mu ndime ya 12 akuti, “Iye wakukhala ndi Mwana ali nao moyo; wosakhala ndi Mwana wa Mulungu(God) alibe moyo.” Mwanjira ina, iye amene amakhulupilira mu zinthu zimene Mwana anachita pa dziko lapansi: Kubatiza Kwake, ndi kufa pa Mtanda, komanso kuuka Kwake, ali ndi moyo wosatha. Koma iye amene amasiya ngakhale chimodzi cha zimenezi sadzakhala ndi moyo, ngakhalenso iye sadzaomboledwa.
Mtumwi Yohane anasiyanitsa anthu a God potengera pa chikhulupiliro chao mu zinthu zimene Yesu anachita: madzi, mwazi, ndi Mzimu Woyera. Zinthu zimenezi zimatiuza ife ngati iwo ali ndi Mau mwa iwo. Iye amazindikira owomboledwa ndi chikhulupiliro chao m’madzi a ubatizo wa Yesu, mwazi Wake, ndi Mzimu Woyera.
Iwo Amene Sanabadwe Mwatsopano Sangasiyanitse pakati pa Nkhosa ndi Mbuzi
| Kodi ndindani amene angasiyanitse pakati pa owomboledwa ndi osawomboledwa? |
| Iye amene ndi obadwa mwatsopano |
Mtumwi Yohane momveka bwino anazindikira olungama amene anaomboledwa. Mtumwi Paulo anazindikiranso. Kodi atumiki a God amasiyanitsa bwanji pakati pa nkhosa ndi mbuzi? Kodi iwo amasiyanitsa bwanji atumiki oona a God ndi onamizira? Iwo amene aomboledwa pokhulupilira mu madzi ndi mwazi wa Yesu amalandira mphamvu ya kuona.
Kaya munthu ndi mbusa, mlalaki, kapena mkulu wa mpingo, ngati iye sangasiyanitse pakati pa nkhosa ndi mbuzi, iye sanaomboledwe mwini, ndipo iye alibe moyo mwa iye. Koma iwo amene awomboledwadi angaone kusiyana. Iwo amene alibe moyo mwa iwo okha sangaone kusiyana ngakhalenso kuzindikira uko.
Zili ngati kusiyanitsa mitundu yosiyana mu m’dima. Chobiriwira ndi chobiriwira ndipo choyera ndi choyera. Ngati inu mwatseka maso anu simungaone ngakhalenso kuzindikira mitundu.
Koma iwo amene maso awo ndi otseguka angazindikire ngakhale kusiyana kochepa kwambiri mu mtundu. Iwo anganene kuti chobiriwira ndi chiti komanso choyera ndi chiti. Mofanana, pali kusiyana kodziwikiratu pakati pa owomboledwa ndi iwo amene sanaomboledwe.
Ife tiyenera kulalikira uthenga wabwino wa chiombolo, uthenga wabwino wa madzi, mwazi, ndi Mzimu Woyera. Ife tiyenera kunyamuka ndi kuwala. Pamene ife tasonkhanitsa anthu mozungulira ife kuti tilalikire chikhulupiliro, ife sitimalankhula ndi mau a munthu. Mu Baibulo, 1 Yohane 5 amafotokoza tanthauzo lake. Ife tiyenera kufotokoza izo pang’ono pang’ono kuti pasakhale chisokonezo.
Mau amene ife tikulalikira, ndiye kuti, mau a madzi, mwazi, ndi Mzimu Woyera wa Yesu, ndi kuunika kwa chiombolo. Kupanga ‘madzi’ a Yesu kudziwika kwa anthu ndi kuwala kwambiri. Kupanga ‘mwazi’ wa Yesu kudziwika kwa anthu ndi kuwala kwambiri. Ife tiyenera kunena momveka bwino kuti pasakhale munthu pa dziko lapansi amene sadziwa zimenezi.
Ngati owomboledwa sanyamuka ndi kuwala, anthu ambiri adzafa opanda chiombolo, ndipo God sadzakondwera. Iye adzatitcha ife kuti ndife atumiki aulesi. Ife tiyenera kufalitsa uthenga wabwino wa madzi ndi mwazi wa Yesu.
Chifukwa chimene ndi kubwereza ndekha kawiri kawiri ndi chakuti ubatizo wa Yesu ndi wofunika kwambiri ku kupulumutsidwa kwathu. Pamene ife tikulankhula kwa ana, ife tiyenera kufotokoza zithu mobwereza bwereza, kudutsa mu mfundo iliyonse kuwonetsetsa kuti iwo amvetsetsa.
Ngati ife tikanayesa kuphunzitsa munthu wosaphunzira, ife makamaka tikanayamba ndi zilembo. Kenako ife pang’ono pang’ono tikanamuphunzitsa iye molembera mau ndi zilembo zimenezi. Pamene iye wakwanitsa kuika mau pamodzi monga ‘chilango’, ife tikanayamba kufotokoza tanthauzo la mau amenewa. Umu ndendende ndi momwe ife tiyenera kulankhulira kwa anthu za Yesu kuwonetsetsa kuti iwo amvetsetsadi.
Ife tiyenera momveka bwino kufotokoza ubatizo wa Yesu. Iye anadza m’dziko lino lapansi mwa madzi, mwazi, ndi Mzimu Woyera. Ndi kupemphera kuti inu mudzakhulupilira mwa Yesu monga Mpulumutsi wanu ndi kuomboledwa.
Chiombolo cha madzi ndi Mzimu Woyera chimachokera ku chikhulupiliro mu ubatizo wa Yesu, mwazi pa Mtanda, ndi chikhulupiliro chakuti Yesu ndi God, Mpulumutsi wathu.
Ulaliki uwu ukupezekanso mu mtundu wa ebook. Dinani pachikuto cha buku pansipa.