(1 Yohane 1:9)“Ngati tibvomereza macimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire macimo athu, ndi kutisambitsa kuticotsera cosalungama ciri conse.”
UTHENGA WA MWAZI NDI THEKA LA UTHENGA
Kodi tingalowe mu ufumu wa kumwamba kudzera mu uthenga wa mwazi okha?
Ai. Tiyenera kukhulupilira mu uthenga wabwino wathunthu (uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu).
1 Yohane 1:9 ikugwiritsidwa ntchito ku olungama okha. Ngati ochimwa amene sanaomboledwebe akufuna kutetezera machimo ake a tsiku ndi tsiku malingana ndi mawu andimeyi ndi kuvomereza zolakwa zake, machimo ake sangachosedwe. Kodi mukuona zimene ndinena apa? Ndimeyi siikugwiritsidwa ntchito ku ochimwa amene sanabadwe mwatsopano.
Muli ambiri m’dzikoli amene sanabadwe mwatsopano, koma amatenga ndimeyi ya 1 Yohane ndime yoyamba ndi kupemphera ndi kulapa machimo awo, kuyembekezera chikhululukiro.
Koma kodi munthu amene sanabadwe mwatsopano angaomboledwe kwathunthu kumachimo ake kudzera mu mapemphero akulapa? Iyi ndi ndemanga yofunikira imene tiyenera kuiganizira ndi kuifotokoza tisanapitirire.
Musanawerenge 1 Yohane, muyenera kuganiza ngati mtumwi Yohane anali munthu wolungama kapena wochimwa. Ndiloreni ndikufunseni funso losatira. Kodi mtumwi Yohane anali munthu wolungama amene anabadwa mwatsopano mwa kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, kapena anali wochimwa?
Ngati mukuti mtumwi Yohane anali wochimwa, mukulakwitsa pabaibulo mu chikhulupiliro chanu. Ngati mtumwi Yohane anali munthu wolungama amene anabadwa mwatsopano pamene anakhulupilira mwa Yesu, zikuonetseratu poyera kuti chikhulupiliro chake chanali chosiyana ndi chanu. Muyenera kukhala ndi chikhulupiliro chofanana ndi cha mtumwi Yohane.
Ndiloreni ndikufunseni funso lina. Kodi mtumwi Yohane anali kulemba makalatawo ku olungama kapena ku ochimwa? Mtumwi Yohane anali kulembela makalatawo kuolungama.
Pachifukwa ichi, ngati ochimwa amene sanabadwe mwatsopano atenga mawu a 1 Yohane 1:8-9 ndi kuwagwiritsa ntchito pa iwo, chikanakhala cholakwika. Ngati mufuna kukhala olungama, vomerezani machimo anu pamaso pa Mulungu ndipo khulupilirani mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Kenako Ambuye adzatsuka machimo anu onse mwa uthenga wabwino umene unatsuka kale machimo adziko.
Chikhulupiliro cha mtumwi Yohane chili motere. Mu 1 Yohane ndime ya 5 iye akuti ali ndichikhulupiliro mu “madzi, mwazi, ndi Mzimu.” Kodi mukhulupilira mwa Yesu Kristu amene anabwera mwa madzi, mwazi, ndi Mzimu? Kodi mumakhulupilira Yesu amene anabwera mwa Mtanda okha, kapena mwa ubatizo Wake, mwazi Wake, ndi Mzimu?
Kodi mungalowe mu ufumu wa Kumwamba mwa kukhulupilira mu uthenga wa mwazi okha? Ngati chikhulupiliro chanu chili mu uthenga wa mwazi okha pa Mtanda, mukudziwa theka lokha la uthenga. Ngati mukukhulupilira mu mwazi okha wa pa Mtanda, nzosakaikitsa m’dzazipeza nokha mukupemphera chikhululukiro tsiku ndi tsiku. Mwai ndi wakuti mukukhulupilira kuti machimo anu angatsukidwe mwa kukhulupilira mophweka kudzera mu mapemphero akulapa.
Koma kodi machimo anu angatsukidwe ngati mukukhulupilira mu mwazi wa pa Mtanda okha, kulapa ndi kupempherera chikhululukiro tsiku ndi tsiku? Ngati ndinu m’modzi wa anthu otere, ndiye kuti machimo anu adzakhalilira m’mitima yanu, chifukwa kulibe munthu amene angatsuke machimo ake kudzera mu chikhulupiliro cha mu mwazi wa pa Mtanda okha, kapena mwa mapemphero akulapa a tsiku ndi tsiku. Ngati ndinu m’modzi wa anthu otere, ndiye kuti simukudziwabe za uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, ndipo chikhulupiliro chanu n’chosakwanira.
Mtumwi Yohane anali obadwa mwatsopano chifukwa anakhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi, mwazi ndi Mzimu. Koma inu mukhulupilira mu mwazi okha wa pa Mtanda. Ngati simudziwa bwino za uthenga wabwino inu nokha, kodi mungatsogolere motani ena kuchipulumutso? Inu nokha sindinu obadwa mwatsopano, koma mukufuna kuphimba machimo anu kudzera mu mapemphero akulapa. Njirayi siidzakutengerani kulikonse.
Ngakhale munthu angapemphere ndi kulapa motani, machimo ake sangatsukidwe mu mtima mwake. Ngati nthawi zina mumamva kuti mwina mwake machimo anu atsukidwa, ndi maganizo chabe komanso mphamvu za zilakolako zanu. Ngati mukupemphera ndi kulapa, mungakhonze kumva kutsitsimutsidwa kwa tsiku limodzi kapena chonchi. Koma simungakhale omasuka kumachimo anu m’njirayi.
Ochimwa amapemphera ndi kulapa, kuyembekezera kuti apulumutsidwe kumachimo awo. Ichi n’chifukwa chake ndi ochimwabe angakhale anakhulupilira mwa Yesu kwa nthawi yaitali. Sadziwa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Ngati mukukhulupilira mwa Yesu koma simunabadwebe mwatsopano, mungakhale m’modzi wa anthuwa. Ngati mukufuna kutetezera machimo anu mwa kupemphera ndi kulapa tsiku ndi tsiku, uwo ndi umboni wapoyera kuti simunabadwe mwatsopano. Muyenera kusankha kaya kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu monga m`mene Mtumwi Yohane anachitira, kapena kuika chikhulupilira chanu mu maganizo ndi zilakolako zanu. Chimodzi n’choonadi cha poyera, ndipo china sichoonadi ai.
Uthenga wabwino woona molingana ndi Baibulo ndi wakuti Yesu anabatizidwa ndipo anachotsa machimo adziko kamodzi kokha ndipo analandira chiweruzo cha ochimwa onse pa Mtanda. Ngati muthu wina akukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi imfa Yake pa Mtanda, adzapulumutsidwa kamodzi ku machimo ake onse. Kumbali ina, ngati munthu wina akufuna kutsuka zolakwa zake kudzera mu mapemphero akulapa, iye sadzamasulidwa kumachimo ake. Kodi mukuganiza kuti mungakumbukire machimo anu onse a tsiku ndi tsiku? Kodi Mulungu amasamalako za machimo amene simunalape? Kodi mapemphero anu akulapa ndimayankho olondola amavuto a machimo anu a tsiku ndi tsiku? Yankho lokhalo la mafunsowa ndi ai.
KULAPA KOONA NDI CHOLINGA CHA KUVOMEREZA
Kodi malire akuvomereza ndi chiyani ndi nchito zabwino?
Ngakhale kuti tikuyenera kuvomereza machimo athu miyoyo yathu yonse, si tingapulumutsidwe mwa kungovomereza chabe zolakwa zathu ndi kugwira nchito zabwino.
Kulapa mu Baibulo chikutanthauza kutembenuka kuchoka kuchikhulupiliro cholakwika kupita kuchikhulupiliro choona, ndipo ku olungama chikutanthauza kudzindikira zolakwa za munthu wina ndikubwerera ku kuunika kwa uthenga wabwino.
Ngati ndiwe ochimwa tsopano, uyenera kuvomereza motere. “Okondedwa Mulungu, ndachimwa ndipo ndiyenera kutumizidwa kugehena. Koma Ndikufuna kupulumutsidwa kumachimo anga. Chonde ndipulumutseni kumachimo anga onse. Sindinabadwebe mwatsopano, ndipo ndikudziwa kuti ndiyenera kugehana.” Uku ndikuvomereza koyenera.
Kenako kodi ndikuvomereza kwa mtundu otani kumene obadwa mwatsopano ayenera kuchita? “Okondedwa Mulungu, ndachimwa uchimo wakusatira za thupi langa. Ndikhulupilira kuti Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi ndipo anandipulumutsa kumachimo anga onse, ngakhalenso machimo amene ndachita apa, pamene ndinayenera kufa chifukwa cha machimo anga. Ndithokoza Ambuye kuti Iye andipulumutsa kudzera mu madzi ndi mwazi.” Kuvomereza kwa obadwa mwatsopano ndi aja sanabadwe mwatsopano n’kosiyana.
Tonse tiyenera kukhala ndichikhulupiliro chofanana ndi cha mtumwi Yohane. Ngati mufuna kubisa machimo anu kumbuyo kwa kuvomereza kumene ndi kwa olungama, ndiye kuti si mudzapulumutsidwa ku imfa, imene ndi mphoto yauchimo.
Ochimwa onse amene sanabadwebe mwatsopano ayenera kuleka kubisala kumapemphero akuvomereza ndipo ayambe kukhulupilira mu uthenga wabwino woona wa madzi, mwazi ndi Mzimu. Ayenera kuphunzira chikhulupiliro cha mtumwi Yohane ndipo potero apeze chipulumutso.
Ochimwa sadzindikira kuopsya kwa chiweruzo cha machimo awo m`mene chidzakhalira. Chimo loopsya kwambiri pamaso pa Mulungu ndi kusakhulupilira mu uthenga wabwino wakubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.
Onse amene amakhulupilira mwa Yesu koma sanabadwebe mwatsopano ayenera kuvomereza kwa Mulungu, “Ambuye, Ndine ochimwa oyenera kuponyedwa m’moto oyaka wa gehena,” ndipo sayenera kunenena, “Ambuye, chonde tsukani machimo anga.” Pamene ochimwa watenga mu mtima mwake uthenga wabwino wakuti Yesu anamupulumutsa iye kudzera mu ubatizo Wake mu Yordano ndi mu mwazi Wake pa Mtanda, angamasulidwe kumachimo ake onse. Uwu ndi mtundu wa kuvomereza kumene ochimwa ayenera kuchita kuti apulumutsidwe kumachimo ake onse pamaso pa Mulungu.
Ochimwa ayenera kungovomereza kuti sanabadwebe mwatsopano ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Kenako iye adzapulumutsidwa kamodzi kokha. Mwa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, chipulumutso cha ochimwa onse chinakwaniritsidwa. “Ndipo palibe cipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo” (Macitidwe a Atumwi 4:12). Mulungu anapulumutsa ochimwa onse kumachimo awo pakulola Mwana Wake, Yesu, kubatizidwa ndi Yohane Mbatizi ndi kufa pa Mtanda.
Ambuye anatsuka machimo onse amene anthu amachita mwa thupi lawo ndi mitima yawo kuchokera pakubawa kwawo mpaka kufa kwawo. Tiyenera kukhulupilira mu uthenga wabwino woona kuti tipulumuke. Ndiyo njira yokhayo imene tingamasulidwe kumachimo athu onse ndi kukhala woyeradi. Tingakhale wolungama kamodzi kokha ngati tikukhulupilira mu uthenga wabwino woona wa madzi ndi Mzimu.
Yesu anabatizidwa, anachotsa machimo adziko, nawalipira pa Mtanda mwa moyo Wake, anaukutsidwa patsiku lachitatu ndipo tsopano akukhala kuzanja lamanja la Mulungu. Ichi n’choonadi chomaliza.
Tonse tiyenera kuchita kuvomereza uku. “Ambuye, sindingaleke koma kuchimwabe mpaka patsiku la kufa Kwanga. Ndinabadwa ochimwa kuchoka m’mimba mwa amai anga, ndipo ndili ndi mulandu wa machimo onse ndachita, ndiyenera kuponyedwa m’moto oyaka wa gehena. Pacifukwa ichi, Ndikufuna kukhulupilira mwa Yesu, amene anabwera mwa madzi, mwazi, ndi mwa Mzimu ndi kukhala Mpulumutsi wanga.”
Monga m`mene kunalembedwa mu Mateyu m’ndime ya chitatu, Yesu anachotsa machimo adziko, kuphatikizapo machimo timachita mpaka patsiku lakufa kwathu, pamene Iye anabatizidwa mu Mtsinje wa Yordano. “Ndipo mudzazindikira coonadi , ndipo coonadi cidzakumasulani” (Yohane 8:32).
Kukanakhala kuti Yesu anatipulumutsa kumachimo obadwa nawo okha ndi kutiuza kuti tithetse bvuto la machimo athu a masiku onse pa ife tokha, tikanakhala m’chisoni chosatha. Koma Yesu anatimasula kumachimo athu onse kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi. Kodi tingade nkhawa za chiyani? Ngati tikhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda, ndi kuthokoza Ambuye, Mzimu umakhala mkati mwa mitima yathu.
Kodi mumakhulupilira mwa Yesu? Kodi mumakhulupilira kuti Mzimu ukukhala mwa inu? Machimo anu onse anaperekedwa pa Yesu pamene anachotsa uchimo wadziko kudzera mu ubatizo Wake. Pambuyo pake Iye anaweruzidwa pa Mtanda chifukwa cha machimo athu, kutimasula ife kuchionongeko chosatha. Uwu ndiwo uthenga wabwino woona.
KUVOMEREZA KWA OLUNGAMA
Kodi kuvomereza koona kwa olungama n’kotani?
Kuvomereza kuti amachimwa tsiku ndi tsiku koma kukhala ndi chikhulupiliro m’choona chakuti Yesu anachotsa machimo awo atsiku ndi tsiku zaka zikwi ziwiri (2000) zapitazo.
1 Yohane 1:9 ikuti, “Ngati tibvomereza macimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire macimo athu, ndi kutisambitsa kuticotsera cosalungama ciri conse.” Ichi chitanthauza kuti munthu amene wafuna kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ayenera kuvomereza machimo ake, mwa kunena kuti, “Ambuye, sindingaleke koma kuchimwa mu moyo wanga wonse koma ndikudziwa kuti sindingapulumutsidwe kumachimo anga onse mwa mapemphero achikhululukiro. ndikhulupilira kuti mphoto yauchimo ndi imfa ndipo palibe china kuchotsako ubatizo wa Yesu ndi kupachikidwa Kwake kungatsuke machimo anga onse. Ndikuvomera kuti ndachimwa lero koma ndikhulupilira Yesu anachotsa kale uchimo umene ndachita lero pa Yordano zaka zikwi ziwiri (2000) zapita.” Ngati munthu otero akupemphera m’njirayi, vuto lamachimo a m’chikumbumutima chake lidzatha mwa kamodzi.
Wonse amene anabadwa kale mwatsopano ayenera kuvomereza machimo awo okha. Iwo angotsimikiza kokha kuti Yesu anachotsa kale machimo alionse amene akuchita. Chifukwa Yesu anabatizidwa ndi kufera ochimwa zaka zikwi ziwiri (2000) zapita, ngakhale angakhale ofoka bwanji, machimo awo onse anachotsedwa kwathunthu.
Ndime imene tawerenga tsiku lalero ndiyabwino kwa anthu olungama. Koma ngati ochimwa atenga ndimeyi ndi kuigwiritsa ntchito mosayenera, azazipeza mu gehena. Komabe, ndi imodzi yandime zogwiritsidwa ntchito molakwika mu Baibulo. Kwa nthawi yaitali yabweretsa kusamvana pakati pa Akristu.
Pali mwambi wakuti dotolo osadziwa bwino-bwino angaphe odwala ake. Pamene dotolo osadziwa bwino-bwino ayetsetsa kuchita chimene iye sakudziwa, iye angamalizire pakupha wodwala wake.
Ndilamulo la moyo kuti munthu ayenera kuphunzitsidwa bwino-bwino kuti akhale kaswiri kuti achite bwino ntchito zake. N’chimodzi-modzi chikhulupiliro cha dziko. Onse aja amene aphunzitsa mawu a Mulungu ayenera kuonetsa choonadi monga momwe chinalebedwa molondola ndiponso momveka, ndipo amene amaphunzira kwaiwo ayenera kukhala ndi chikhulupiliro mu zimene aphunzitsidwa.
Ngati alaliki aphunzitsa owasatira awo ziphunzitso zolakwika, kapena ngati okhulupilirawo akuphunzira Baibulo molakwika, chizawabweretsera chabe chiweruzo ndi gehena onse a iwo. Obadwa mwatsopano okha angaphunzitse Baibulo molondola. Ngakhalenso mankwala abwino angaphe odwala ngati apatsidwa mosalondola bwino, ndichimodzi-modzi ndi kuphunzitsa ndi kuphunzira mawu a Mulungu. Ndi chofunikira ngati moto mu moyo wathu. Monga momwe moto ungabweretsere chionongeko ngati waikidwa m’manja a ana, mawu a Mulungu angabweretse chionongeko choopsya m’manja mwa anthu osayenera.
Tiyenera kudziwa kusiyana pakati pakuvomereza kwa olungama ndi kwa ochimwa. 1 Yohane 1:9 ndi yaolungama. Ngati munthu olungama avomereza machimo ake mwa chikhulupiliro pamaso pa Ambuye, iye amamasulidwa ku machimowo chifukwa Yesu anachotsa kale uchimo wonse zaka zikwi ziwiri (2,000) zapita.
Ndicholakwika ngati ochimwa akhulupilire kuti machimo awo anachotsedwa nthawi iliyonse akapemphera pachikhululukiro. Ngati munthu ndi osabadwa mwatsopano, kodi machimo ake angatsukidwe mwa kulapa kokha?
Mulungu ndi olungama. Iye anatumiza Mwana Wake wobadwa yekha padzikoli ndipo anamlola Iye kuchotsa machimo onse adziko kudzera mu ubatizo Wake ndi mu mwazi Wake pa Mtanda. Pachifukwa ichi, ngati munthu olungama akuvomereza machimo ake, Mulungu amamuuza iye kuti Yesu anachotsa kale uchimo onse wa dziko zaka zokwanira zikwi ziwiri (2,000) zapitazo. Munthu otero mwakutero ndi m`mene amatsimikizira kuti iye alibe uchimo mu mtima mwake, ngakhale kuti thupi lake likuchimwabe.