• All e-books and audiobooks on The New Life Mission website are free
  • Explore multilingual sermons in global languages
  • Two new revised editions in English have been released
  • Check out our website translated into 27 languages
Search

Sermons

Mutu 3: Uthenga Wabwino wa Madzi ndi Mzimu Woyera

[3-4] Ubatizo wa Yesu Ndi Chifaniziro cha Chipulumutso cha Ochimwa (1 Petro 3:20-22)

Ubatizo wa Yesu Ndi Chifaniziro cha Chipulumutso cha Ochimwa (1 Petro 3:20-22)
(1 Petro 3:20-22)
“Imene inakhala yosamvera kale, pamene kuleza mtima kwa Mulungu(God) kunalindira, m’masiku a Nowa, pokhala m’kukonzeka chingalawa, m’menemo owerengeka, ndiwo amoyo asanu ndi atatu, anapulumutsidwa mwa madzi; chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho Ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbumtima chokoma kwa Mulungu(God), mwa kuuka kwa Yesu Khristu; amene akhala padzanja lamanja la Mulungu(God), atalowa mu Mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zonse zimgonjera.” 
 
 
Kodi ife tinakhala olungama kudzera mu chiyani?
Kudzera mu chisomo cha God 
 
Ife tinabadwa pa dziko lino lapansi, koma tisabadwe God anatidziwa kale ife. Iye anadziwa kuti ife tidzabadwa ochimwa ndi kupulumutsa tonse a ife okhulupilira kudzera mu Ubatizo Wake, umene unachotsa machimo onse a dziko lapansi. Iye anapulumutsa okhulupilira onse ndi kupanga iwo onse kukhala anthu Ake.
Zonse zimenezi ndi zotsatira za chisomo cha God. Monga kwanenedwa mu Masalimo 8:4 kuti, “Munthu ndani kuti mumkumbukira?” Iwo amene apulumutsidwa ku machimo onse ndi olandira a chikondi Chake chapadera. Iwo ndi ana Ake.
Kodi ife tinali chiyani, amene tinakhulupilira kokha mu mwazi Wake ndi Mzimu Woyera, tisanakhale ife ana a God, tisanakhale ife olungama komanso tisanapulumutsidwe ndi kupatsidwa mphamvu zoitana Iye Atate? Ife tinali ochimwa, ochimwa wamba amene tinabadwa kuti tikhale m’dziko lino lapansi kwa zaka 60-70 kapena zaka 70-80 ngati tili athanzi.
Ife tisanatsukidwe ku machimo athu, komanso pamene ife tinalibe chikhulupiliro mu uthenga wabwino wa Ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, ife tinali anthu osalungama amene tinali otsimikiza kuti tiwonongeka.
Mtumwi Paulo ananena kuti chinali chifukwa cha chisomo Chake kuti iye anali chimene iye anali. Ndi chifukwa cha chisomo Chake kuti ife tili chomwe tili tsopano. Ife tikuthokoza Iye chifukwa cha chisomo Chake. Mlengi anadza ku dziko lino lapansi ndi kutipulumutsa ife, kutipanga ife ana Ake, anthu Ake. Ife tikuthokoza Iye chifukwa cha chisomo cha chipulumutso cha madzi ndi Mzimu Woyera.
Kodi ndi chifukwa chiyani Iye amatilola ife kuti tikhale ana Ake, olungama? Kodi chifukwa chakuti ndife okongola m’maonekedwe? Kodi ndi chifukwa chakuti ndife oyenera kwambiri? Kapena ndi chifukwa chakuti ndife abwino kwambiri? Tiyeni tiganizire icho ndi kupereka mathokoza pamene ndi poyenera. 
Chifukwa ndi chakuti God anatilenga ife kuti atipange ife anthu Ake ndi kutilola ife kuti tikhale mu ufumu wa kumwamba ndi Iye. God anatipanga ife anthu Ake kutilola ife kuti tikhale ndi Iye kwamuyaya. Palibe chifukwa china chimene God anatidalitsira ife ndi moyo wamuyaya. Si zoona kuti Iye anatipanga ife kukhala anthu Ake chifukwa ndife owoneka bwino, oyenera kwambiri, kapena okhala moyo waukhondo kuposa zolengedwa Zake zina. Chifukwa chokha ndi chakuti Iye amatikonda ife. 
“Chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho Ubatizo” (1 Petro 3:21). “M’menemo owerengeka, ndiwo amoyo asanu ndi atatu, anapulumutsidwa mwa madzi” (1 Petro 3:20).
Ochepa okha, m’modzi wa mzinda komanso awiri a m’banja apulumutsidwa. Kodi ndife abwino kuposa ena? Ayi, ndi pang’ono pomwe. Si ndife apadera konse, koma ife tapulumutsidwa mulimonse kudzera mu chikhulupiliro chathu m’madzi ndi Mzimu Woyera. 
Ndi chozizwitsa pakati pa zozizwitsa kuti ife tapulumutsidwa, komanso ndi mphatso yopanda malire ndi dalitso lochokera kwa God kuti ife tingamutche Iye Atate wathu, Ambuye wathu. Ife sitingakane chimenechi. Kodi ife tikanamutcha bwanji Iye Atate wathu kapena Ambuye wathu ngati ife tikanakhalabe ochimwa?
Pamene ife taganizira za choona chakuti ife tapulumutsidwa, ife timadziwa kuti ndife okondedwa ndi God. Ife tikanabadwa ndi kufa popanda tanthauzo lililonse ndipo tonse tikanapita ku gahena kukanapanda chikondi Chake, madalitso Ake. Ife timathokoza God mobwereza bwereza chifukwa cha madalitso Ake komanso chikondi chinatipanga ife kukhala ana Ake komanso oyenera m’maso Mwake.
 
 

Chipulumutso Chamtengo Wapatali hoperekedwa kwa Ife kudzera mu Ubatizo wa Yesu 

 
Kodi ndi chifukwa chiyani anthu mu nthawi ya Nowa anaonongeka?
Chifukwa chakuti iwo sanakhulupilire m’madzi (Ubatizo wa Yesu).
 
“Chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho Ubatizo.” Kwalembedwa mu 1 Petro kuti anthu asanu ndi atatu okha anapulumutsidwa kudzera m’madzi. Kodi ndi anthu angati amene analipo mu nthawi ya Nowa? Ife tilibe njira yodziwira kuti analipo angati, koma tiyeni tiyerekeze kuti analipo okwanira miliyoni imodzi. Anthu 8 okha m’banja la Nowa mwa miliyoni imodzi anapulumutsidwa. 
Chiwerengero chikanakhala pafupifupi chofanana lero. Iwo amanena kuti kuli anthu oposa mabiliyoni 8 padziko lapansi tsopano. Kodi ndi anthu angati amene atsukidwa ku machimo ao mwa iwo amene amakhulupilira mwa Yesu lero? Ngati ife tingaone mu mzinda umodzi chabe, mungakhale ochepa kwambiri a iwo.
Mu mzinda umene uli ndi anthu pafupifupi 250,000, kodi ndi angati mwa iwo amene angakhale owomboledwa ku machimo ao―mwina 200? Ndiye kodi chiwerengero chingakhale bwanji? Zingatanthauze kuti ochepera m’modzi mwa chikwi adalandira dalitso la chiombolo.
Kwayerekezedwa kuti muli pafupifupi Akristu 12 miliyoni mu Korea, kuphatikiza Achikatolika. Mwa amenewa, kodi ndi angati mwa iwo amene abadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu Woyera? Ife tiyenera kukumbukira kuti kunali anthu 8 okha amene anapulumutsidwa mwa chiwerengero chonse cha dziko lapansi mu nthawi ya Nowa. fe tiyenera kudziwa ndi kukhulupilira kuti Yesu anatsuka machimo a iwo onse amene amakhulupilira mu Ubatizo Wake, omwe Iye anatengera uchimo onse. 
Palibe ambiri amene amakhulupilira kuti Yesu anatiombola ife tonse ndi Ubatizo Wake ndi mwazi Wake pa Mtanda. Yang’anani pa chithunzi chotchuka cha ‘Kuuka kwa Yesu.’ Kodi ndi anthu angati oukitsidwa amene akuonetsedwa pamenepo? Kodi ndi angati mwa iwo amene ndi azaumulungu?
Lero, muli azaumulungu ambiri m’dziko lapansi, koma ife timapeza ochepa kwambiri amene amadziwa ndi kukhulupilira mu Ubatizo wa chiombolo. Azaumulungu ena amanena kuti chifukwa chimene Yesu anabatizidwira chinali chakuti Iye anali wodzichepetsa, ndipo ena amanena kuti Iye anabatizidwa kuti akhale monga anthu ena.
Koma kwalembedwa m’Baibulo kuti atumwi onse, kuphatikiza Petro ndi Yohane, anachitira umboni za kusamutsa kwa machimo athu kupita kwa Yesu kudzera mu Ubatizo Wake, ndipo ife timakhulupiliranso icho. 
Atumwi anachitira umboni m’Malemba kuti machimo athu anaperekedwa pa Yesu ndi Ubatizo Wake. Ndi umboni wodabwitsa ku chisomo cha God kuti ife tingapulumutsidwe pokhulupilira kokha mu uwo.
 
 
Kulibe ‘Mwina’ za Ubatizo wa Chiombolo 
 
Kodi ndindani amalandira chikondi chopanda malire cha God?
Munthu amene amakhulupilira mu Ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake
 
Zipembedzo zonse ndi zotsimikiza za chipulumutso mu zikhulupiliro zao, ndipo anthu ambiri amaganiza kuti Ubatizo wa Yesu ndi chiphunzitso chabe cha gulu la Chikristu. Koma si zoona. Mwa zikwi za mabuku amene ndawerenga, sindinathe kupeza buku lililonse lokhudza chipulumutso limene limafotokoza ubale pakati pa chiombolo mu Ubatizo ndi mwazi wa Yesu ndi chipulumutso. 
Anthu 8 okha anapulumutsidwa pa nthawi ya Nowa. Sindikudziwa kuti ndi angati amene adzapulumutsidwa lero, koma mwina osati ambiri. Iwo amene adzapulumutsidwa ndi iwo amene amakhulupilira mu Ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Poyendera mipingo yambiri, ndazindikira mobwereza bwereza kuti palibe amene akulalikira uthenga wabwino wa Ubatizo wa Yesu, umene ndi uthenga wabwino wa choonadi.
Ngati ife sitikhulupilira mu chiombolo cha Ubatizo ndi mwazi wa Yesu, ndiye kuti ndife ochimwabe. (Zilibe kanthu momwe ife timapitira mokhulupirika ku mpingo.) Ife mokhulupirika tingapite ku mpingo miyoyo yathu yonse. Koma ngati ife tidakali ndi uchimo m’mitima mwathu, ndiye kuti ife tidakali ochimwa.
Ngati ife tapita ku mpingo kwa zaka 50 koma kukhalabe ndi uchimo m’mitima mwathu, ndiye kuti chikhulupiliro cha zaka 50 si kanthu koma bodza. Ndi kwabwino kwambiri kukhala ndi tsiku limodzi lokha la chikhulupiliro choona. Mwa iwo amene amakhulupilira mwa Yesu, okhawo amene amakhulupilira molondola mu tanthauzo la Ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake adzalowetsedwa mu ufumu wa kumwamba. 
Chikhulupiliro choona ndi kukhulupilira mu choona chakuti Mwana wa God adatsika ku dziko lino lapansi ndipo adabatizidwa kuti achotse machimo onse a dziko lapansi. Ndi chikhulupiliro chimenechi chimene chimatitsogolera ife ku ufumu wa kumwamba. Ife tiyeneranso kukhulupilira kuti Yesu anakhetsa mwazi pa Mtanda chifukwa cha inu ndi ine. Ife tiyeneranso kudziwa zimenezi kuti timuthokoze Iye. 
Kodi ndife chiyani? Ndife ana a God amene Iye anapulumutsa ndi Ubatizo Wake ndi mwazi. Kodi ife sitingamuthokoze bwanji Iye? Yesu anabatizidwa mu Yordano pamene Iye anali ndi zaka 30 kuti atipulumutse ife. Mwa zimenezi, Iye anachotsa machimo athu onse ndi kulandira chiweruzo chifukwa cha ife pa Mtanda. 
Pamene ife taganizira za icho, ife sitingakwanitse koma modzichepetsa kuthokoza Iye. Ife tiyenera kudziwa kuti zonse zimene Yesu anachita m’dziko lino lapansi zinali za chipulumutso chathu. Choyamba Iye anadza ku dziko lino lapansi. Iye anabatizidwa, anapachikidwa pa Mtanda, anaukitsidwa kwa akufa patatha masiku 3, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la God. 
Chiombolo cha God ndi cha wina aliyense wa ife popanda kuchotsera. Chipulumutso cha Yesu chonse ndi chanu ndi changa. Ife timayamika God chifukwa cha chikondi chake ndi madalitso Ake.
Ife tikudziwa nyimbo ya uzimu imene imaimbidwa motere. “♫Kuli nkhani yokoma. Mwa anthu ambiri m’dziko lapansi, ndine ndekha amene ndili ndi chikondi Chake ndi chipulumutso. Aa chikondi Chake chodabwitsa motani! Chikondi Chake paine, chikondi Chake paine. Pali nkhani yokoma. Mwa anthu ambiri m’dziko lapansi, ndife amene tapulumutsidwa, amene tidasanduka ana Ake. Ife tavala chikondi Chake. Aa chikondi cha God, chisomo cha God. Chikondi Chake chodabwatsa motani! Chikondi Chake pa ine.♫” 
Yesu anadza kudzapulumutsa inu ndi ine, ndipo chiombolo cha Ubatizo Wake ndi cha inunso ndi ine. Uthenga wabwino si nthano chabe, ndi choonadi chimene chimatichotsa ife m’moyo wathu wotopetsa ndi kutipititsa mu ufumu wa God wokongola. Chikhulupiliro ndi ubale pakati pa God ndi ine mwini.
Iye anadza ku dziko lino lapansi kuti atipulumutse ife. Iye anabatizidwa ndi kulandira chiweruzo cha Mtanda kuti atsuke machimo athu.
Kodi ndi dalitso lotani pamene okhulupilirika angatche God Atate wao! Kodi ife tingakhulupilire bwanji mwa Yesu monga Mpulumutsi wathu ndi kupulumutsidwa ku uchimo ndi chikhulupiliro chathu? Zonse ndi zotheka chifukwa cha chikondi chake chopanda malire pa ife. Ife tapulumutsidwa chifukwa cha Iye amene anatikonda ife poyamba. 
 
 

Yesu Anatsuka Machimo Athu onse Kamodzi Kokha

 
“Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m’malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu(God)” (1 Petro 3:18). Yesu Kristu anabatizidwa chifukwa cha chiombolo chathu ndi kufa kamodzi pa Mtanda kuti apulumutse inu ndi ine, osalungama.
 
Kodi ife timapulumutsidwa kamodzi kokha kapena pang’ono pang’ono?
Kamodzi kokha
 
Kuti achotse choyenera kwa ife kuimilira pamaso pa God ku chiweruzo chathu, Iye anafa kamodzi pa dziko lino lapansi. Kuti ife tingakhale mu ufumu wa kumwamba pamaso pa God, Iye anadza ku dziko lino lapansi m’thupi ndi kutsuka motheratu machimo athu onse kamodzi kokha ndi Ubatizo Wake, imfa Yake pa Mtanda, ndi kuuka Kwake.
Kodi inu mukukhulupilira kuti Yesu Kristu anatipulumutsa ife motheratu ndi Ubatizo Wake ndi mwazi? Ngati inu simukhulupilira mu uthenga wabwino wa Ubatizo Wake ndi mwazi, ndiye kuti inu simungapulumutsidwe. Chifukwa chakuti ndife ofooka kwambiri, ife sitingabadwe mwatsopano ngati ife sitikhulupilira kuti Yesu anatsuka motheratu machimo athu onse kamodzi kokha ndi Ubatizo Wake ndi mwazi.
Iye anabatizidwa kuti achotse machimo athu onse ndipo anaweruzidwa pa Mtanda chifukwa cha ife kamodzi kokha. Yesu anatsuka machimo onse a ochimwa kamodzi kokha ndi chiombolo cha Ubatizo Wake ndi mwazi. 
Zikanakhala zosatheka kwa ife anthu kuomboledwa ngati ife timayenera kulapa nthawi zonse pamene tachimwa, kukhala abwino ndi kukhala a chifundo nthawi zonse, ndi kuperekanso zinthu zambiri ku mpingo.
Choncho, chikhulupiliro mu Ubatizo wa Yesu ndi mwazi pa Mtanda ndi choyenera ku chipulumutso chathu. Ife tiyenera kukhulupilira m’madzi ndi mwazi. Ife kwenikweni sitingachite zinthu zabwino kuti tibadwe mwatsopano.
Si zizapanga kalikonse kabwino kugulira zovala zabwino osauka kapena kupereka chakudya chopatsa mudyo kwa abusa. Yesu amapulumutsa okhawo amene amakhulupilira mu Ubatizo Wake ndi mwazi Wake. Ngati ife timakhulupilira kuti God anatipulumutsa ife kudzera mwa Yesu ndi Ubatizo Wake ndi mwazi Wake kamodzi kokha, ife tidzapulumutsidwa.
Ena angaganize kuti ngakhale God ananena zimenezi m’Baibulo, iwo ayenera kuganizirapobe. Izi zili kwa iwo. Koma ife tiyenera kukhulupilira m’Mau Ake monga kwalembedwa. 
Mu Ahebri 10:1-10, kwalembedwa kuti Iye anatipulumutsa ife kamodzi kokha. Ndi zoona kuti God anapulumutsa iwo amene amakhulupilira mu Ubatizo ndi mwazi wa Yesu kamodzi kokha. Ifenso tiyenera kukhulupilira icho motero. “♫ Iye anafa kamodzi, kutipulumutsa ife kamodzi kokha. O abale khulupilirani ndi kupulumutsidwa. Ikani zothodwa zanu pansi pa Ubatizo wa Yesu.♫” Yesu anatipulumutsa ife ku zosalungama zonse ndi machimo kamodzi kokha pobatizidwa kamodzi, kukhetsa mwazi kamodzi. 
“Akuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m’malo mwa osalungama” (1 Petro 3:18). Yesu ndi God wopanda uchimo, amene sanachimwepo. Iye anadza kwa ife m’thupi kuti apulumutse anthu ku machimo ao. Iye anabatizidwa ndi kuchotsa machimo onse a osalungama. Iye anatipulutsa ife ku uchimo ndi zosalungama.
Machimo onse a anthu kuchokera kubadwa kwao kufikira imfa anaperekedwa kwa Yesu pamene Iye anabatizidwa, ndipo onse anapulumutsidwa ku chiweruzo pamene Iye anakhetsa mwazi ndi kufa pa Mtanda. Iye anabatizidwa chifukwa cha ochimwa ndi kufa m’malo mwa ochimwa.
Ichi ndi chiombolo cha Ubatizo Wake. Yesu anapulumutsa tonse a ife amene tinali ochimwa kamodzi kokha. Kodi aliyense wa ife ndi ofooka bwanji! Yesu anaombola machimo athu onse kuchokera ku kubadwa kwathu mpaka imfa ndi kudzipereka Yekha ku chiweruzo pa Mtanda. Ife amene timakhulupilira mwa Yesu tiyenera kukhulupilira kuti Iye anatipulumutsa ife kamodzi kokha ndi Ubatizo Wake ndi mwazi.
Ndife wofooka, koma Yesu si wofooka. Ndife osakhulupirika, koma Yesu ndi okhulupirika. God anatipulumutsa ife kamodzi kokha. “Pakuti Mulungu(God) anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha” (Yohane 3:16). God anatipatsa ife Mwana Wake wobadwa yekha. Iye adapanga mwana Wake kubatizidwa kuti apereke machimo onse a dziko lapansi pa Iye kuti Iye alandire chiweruzo cha anthu onse.
Kodi ndi chipulumutso chidabwitsa bwanji chimenechi! Kodi ndi chikondi chodabwitsa bwanji chimenechi! Ife tikuthokoza God chifukwa cha chikondi Chake ndi chipulumutso. God amapulumutsa iwo amene amakhulupilira m’madzi ndi mwazi wa Yesu: Ubatizo wa Yesu ndi choona chakuti Yesu ndi Mwana wa God.
Choncho, iwo amene amakhulupilira mwa Yesu angapulumutsidwe pokhulupilira mu choonadi cha Ubatizo ndi mwazi wa Yesu ndi kukhala ndi moyo wosatha monga olungama. Ife tonse tiyenera kukhulupilira icho.
Kodi ndindani anatipulumutsa ife? Kodi ndi God anatipulumutsa ife, kapena chinali chimodzi cha zolengedwa Zake chimene chinatipulumutsa ife? Anali Yesu, amene ndi God, amene anatipulumutsa ife. Ife tinapulumutsidwa chifukwa ife timakhulupilira mu chiombolo cha God, ndipo ichi ndi chipulumutso cha chiombolo.
 
 
Yesu Ndi Ambuye wa Chipulumutso
 
Kodi tanthauzo la ‘Kristu’ ndi chiyani?
Wansembe, Mfumu, komanso Mneneri
 
Yesu Kristu ndi God. Yesu amatanthauza Mpulumutsi, ndipo Kristu amatanthauza ‘munthu amene wadzodzedwa’. Monga Samueli anadzodza Sauli m’Chipangano Chakale, mafumu ankadzodzedwa, ansembe ankadzodzedwa komanso kuti mneneri atumikire ntchito yake ya uneneri, iye ankayenera kudzodzedwa.
Yesu anadza ku dziko lino lapansi ndipo anadzodzedwa ku maudindo atatu: uwo wa Wansembe, Mfumu, komanso Mneneri. Monga Wansembe wa kumwamba, Iye anabatizidwa kuti atengere machimo a munthu pa Iye Mwini. 
Pomvera chifuniro cha Atate Wake, Iye anadzipereka Yekha monga nsembe ya uchimo pamaso pa Atate. “Ine ndine njira, ndi coonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine” (Yohane 14:6). Yesu anapulumutsa iwo a ife amene timakhulupilira mwa Iye potenga machimo athu onse kudzera mu Ubatizo Wake komanso popachikidwa.
“Pakuti moyo wa (thupi—NKJV) ukhala m’mwazi” (Levitiko 17:11). Yesu anakhetsa mwazi pa Mtanda pambuyo pa Ubatizo Wake; motero kupereka moyo Wake pamaso pa God monga mphotho ya machimo athu kuti ife okhulupilira tipulumutsidwe.
Iye anaukitsidwa masiku atatu pamene Iye anafa pa Mtanda ndipo Iye analalikira ku mizimu yotsekeredwa mu ndende. Iwo amene sanapulumutsidwebe ali ngati akaidi a uzimu mu ndende ya uchimo, ndipo kwa iwo, Yesu amalalikira uthenga wabwino wa choonadi, uthenga wabwino wa madzi ndi mwazi. God watipatsa ife uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu Woyera kuti utipulumutse ife. Aliyense amene amakhulupilira mu uwo ndi obadwa mwatsopano.
 
 

Ubatizo ndi Mwazi wa Yesu Zimapulumutsa Ochimwa

 
Kodi ife tingakhake bwanji ndi chikumbumtima chabwino pamaso pa God?
Pokhala ndi chikhulupiliro mu Ubatizo ndi mwazi wa Yesu
 
Yesu Kristu ndi Mpulumutsi wathu, ndipo zachitidwa umboni mu 1 Petro 3:21 kuti, “Cimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbumtima chokoma kwa Mulungu(God).” Madzi a Ubatizo wa Yesu ndi zofunika kwambiri ku chipulumutso cha ochimwa.
Yesu anatsuka machimo a ochimwa onse potenga machimo amenewa pa Iye Mwini kudzera mu Ubatizo Wake. Kodi inu mumakhulupilira mu Ubatizo wa Yesu? Kodi inu mumakhulupilira kuti mitima yathu yatsukidwa moyera ku machimo onse kudzera mu Ubatizo wa Yesu? Mitima yathu yatsukidwa moyera ku machimo onse, koma thupi lathu limachimwabe.
‘Munthu amene waomboledwa’ sizikutanthauza kuti iye sadzachimwanso. Ife timachimwa. Koma mitima yathu imakhala yopanda uchimo chifukwa cha chikhulupiliro chathu mu Ubatizo Wake. Zikutanthauza kuti, “kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbumtima chokoma kwa Mulungu(God)” (1 Petro 3:21).
Popeza Yesu anatsuka machimo anga, komanso popeza God anavomera chiweruzo changa, kodi sindingakhulupilire bwanji mwa Iye? Podziwa kuti Yesu, amene ndi God, anandipulumutsa ine kudzera mu Ubatizo Wake ndi mwazi, kodi sindingakhulupilire bwanji mwa Iye? Ife tinapulumutsidwa pamaso pa God ndipo tsopano zikumbumtima zathu ndi zoyera. Ife sitinganenenso pamaso pa God kuti Yesu sanatsuke motheratu machimo athu, monga ife sitinganenenso kuti God satikonda ife. 
Chikumbumtima chathu chimakhudzidwa kwambiri ndipo icho chimatiuza ife nthawi zonse pamene ife tachita cholakwa. Ngati chikumbumtima chathu chaipidwa ngakhale pang’ono, ife sitingakhale omasuka motheratu ku uchimo popanda kukhulupilira mu Ubatizo wa Yesu. Ndi njira yokhayo imene ife tingakhalire ndi chikumbumtima chabwino.
Pamene chikumbumtima chathu chativuta ife, zikutanthauza kuti chinachake ndi cholakwika. Madzi a Ubatizo wa Yesu amatsuka litsiro lonse la uchimo. Yesu anatenga machimo athu onse ndi Ubatizo Wake ndi kutitsuka ife moyera. Pamene ife kwenikweni takhulupilira zimenezi, zikumbumtima zathunso zingayeretsedwedi. Kodi chikumbumtima chathu chingayeretsedwe bwanji? Pokhulupilira mu Ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Aliyense ali chikumbumtima choipa komanso cha litsiro kuyambira pa kubadwa. Koma ngati ife takhulupilira kuti machimo athu onse anaperekedwa kwa Yesu, ife tingafafanize machimo athu onse.
Ichi ndi chikhulupiliro cha obadwa mwatsopano. Si chinachake chimene inu mumavomereza mwachizindikiro. Kodi chikumbumtima chanu ndi choyera? Kodi ndi choyera chifukwa chakuti inu mwakhala moyo wabwino, kapena ndi choyera chifukwa chakuti machimo anu onse anaperekedwa pa Yesu ndipo inu mumakhukupilira mwa Iye? Ndi kudzera kokha mu chikhulupiliro chimenechi kuti inu mungapeze chikumbumtima choyera.
Pali mau amoyo ndi mau opanda moyo. Kodi chikumbumtima cha anthu onse chingayeretsedwe bwanji? Njira yokhayo imene ife tingakhalire olungama ndi kukhala ndi chikumbumtima choyera ndi kukhulupilira mu chiombolo chonse kudzera mwa Yesu. 
Pamene ife tayeretsedwa pokhulupilira mu Ubatizo Wake, sizikutanthauza kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbu mtima chokoma kwa God. Chifukwa cha chimenecho, Iye anadza ndipo anabatizidwa ndi kufa pa Mtanda ndipo anaukitsidwa kwa akufa ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la God. 
Pamene nthawi yafika, Iye adzabweranso ku dziko lino lapansi. “Adzaonekera pa nthawi yachiwiri, wopanda uchimo, kwa iwo amene amlindirira, kufikira chipulumutso” (Ahebri 9:28). Ife timakhulupilira kuti Iye adzabwera kudzatitenga ife amene tikumuyembekezera Iye, amene timakhulupilira mu Ubatizo Wake ndi mwazi.
 
 
Kuyesa kwa Chipatala cha Chikhulupiliro 
 
Kodi ife tingapulumutsidwe popanda Ubatizo wa Yesu?
Osatheka konse
 
Ife mosayembekezera tidachita Kuyesa kwa Chipatala kochepa pa umodzi wa mipingo yathu. 
Mbusa Park wa mpingo umenewu anauza banja lina kuti mulibe uchimo m’dziko lapansi popanda kutchula tanthauzo la Ubatizo wa Yesu. Mwamuna wa mkaziyo ankakonda kugona mkati mwa ulaliki pamene iye wapita ku mipingo ina chifukwa chakuti abusa onse ankalikila uthenga wabwino posiya chiombolo kudzera mu Ubatizo wa Yesu, motero kukakamiza iye kulapa tsiku lililonse.
Koma ku mpingo umenewo, iye anamvera ku ulaliki ndi maso ake onse otsegula kwambiri chifukwa chakuti iye anamva kuti machimo ake onse anaperekedwa pa Yesu. Zinapanga kukhala zophweka kwa mkazi wake kumukopa iye kuti azibwera naye ku mpingo.
Tsiku lina, iye anakhala mu mpingo ndi kumva Aroma 8:1. “Chifukwa chake tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa (konse—NKJV)” Kenako, iye anaganiza pomwepo kuti, ‘Ah, ngati munthu amakhulupilira mwa Yesu, ndiye kuti iye alibe uchimo. Popeza kuti ndimakhulupilira mwa Yesu, ndinenso opanda uchimo.’
Choncho iye anaimbira lamya mulamu wake ndi amzake ena ambiri m’modzi m’modzi ndi kunena kuti, “Kodi inu muli ndi uchimo mu mtima mwanu? Ndiye kuti chikhulupiliro chanu si cholondola.” Pa chimenechi, Mbusa Park analuza. Mwamunayo sankadziwa za Ubatizo wa Yesu, koma iye anatsimikizira kwa aliyense kuti iye tsopano analibe uchimo.
Kenako banja la linayamba kukhala ndi mavuto. Mkazi wa mwamunayo anali wokhulupilirika kwambiri kuposa mwamuna wake, koma iye ana adakali ndi uchimo mu mtima mwake, pamene mwamuna wake ananena kuti iye anali wopanda uchimo. Mwamunayo adapita ku mpingo nthawi yochopa kokha, koma iye adanena kuti iye anali kale wopanda uchimo.
Mkazi wa mwamunayo anali wotsimikiza kuti onse a iwo anali adakali ndi uchimo m’mitima mwao. Iwo anayamba kulimbana za icho. Mwamunayo analimbikira kuti iye analibe uchimo chifukwa chakuti “Chifukwa chake tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa (konse—NKJV).” Ndipo mkaziyo anatsutsa kuti iye anali adakali ndi uchimo mu mtima mwake. 
Kenako tsiku lina, mkazi wake anaipidwa nazo kwambiri kuti iye anaganiza zopita ndi kukafunsa mbusa zomwe iye ankatanthauza pamene iye ananena kuti machimo ake onse anaperekedwa pa Yesu. 
Choncho tsiku lina utumiki wamadzulo utatha, iye anatumiza mwamuna wake kunyumba ndi kukumana ndi Mbusa Park ndi funso. Iye ananena kuti, “Ndikudziwa kuti mukuyesa kutiuza ife chinachake, koma ndikukhulupilira kuti pali mbali imodzi yofunika imene yabisidwa. Chonde ndiuzeni ine kuti ndi chiyani.” Ndipo Mbusa Park anamuuza iye za kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu Woyera.
Kenako iye anazindikira pomwepo chifukwa chimene kunalembedwa mu Aroma 8:1 kuti, “Chifukwa chake tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa (konse—NKJV).” Iye anakhulupilira pomwepo ndipo anapulumutsidwa. Iye anazindikira pamapeto kuti machimo athu onse anaperekedwa pa Yesu kudzera mu Ubatizo Wake kuti iwo amene ali mwa Kristu asatsutsidwe.
Iye anayamba kumvetsetsa Mau olembedwa. Iye pamapeto pake anapeza kuti mfungulo ku chiombolo unali Ubatizo wa Yesu komanso kuti ife tingakhale olungama kudzera mu chiombolo cha Ubatizo.
Mwamuna wa mkaziyo sanapite kunyumba koma ankamudikira iye panja. Iye anafunsa kuti, “Waombolodwa tsopano?”
Koma iye anamvetsera zimene mbusa wake anauza mkazi wakeyo ndi kukhala osokonezeka mwini. Iye sanamvepo za uthenga wabwino wa Ubatizo wa Yesu. Iye anali wotsimikiza kuti iye analibenso uchimo mu mtima mwake ngakhale popanda Ubatizo wa Yesu. Choncho kunyumba, anatsutsananso.
Nthawi ino, kutsutsana kuja kunatembuka. Mkazi anapanikiza mwanuna ngati iye adali ndi uchimo mu mtima mwake kapena ai. Iye anafunsa iye kuti angakhale bwanji opanda uchimo pamene iye sanakhulupilire mu Ubatizo wa Yesu. Iye anamutsutsa iye kuti ayang’ane mwatcheru mu chikumbumtima chake. Iye anazindikira pofufuza mu chikumbumtima chake kuti iye anali adakali ndi uchimo mu mtima mwake. 
Choncho iye anadza kwa Mbusa Park ndi kuvomereza kuti iye adali ndi uchimo mu mtima mwake. Ndipo iye adafunsa kuti, “Pamene iwo ankaika manja ao pa mutu wa mbuzi ya Azazele, kunali pamene iwo asanaphe iyo, kapena pamene iwo apha iyo.” Iye adali asanamvepo za uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu Woyera. Choncho Iye anali wosokonezeka kwambiri.
Iyo inali mfundo ya Kuyesa kwa Chipatala kwa uzimu kumeneku. Yesu adayenera kubatizidwa kuti machimo onse a dziko lapansi aperekedwe pa Iye. Pokhapo ndi pamene iye akanafa pa Mtanda chifukwa chakuti mphotho ya uchimo ndi imfa.
 “Kodi iwo ankaika manja ao pa mutu wa nyama ya nsembe asanaphe, kapena atapha kale iyo?” Iye anafunsa zimenezi chifukwa chakuti iye anali osokonezeka za kuika manja ndi Ubatizo wa Yesu. Choncho Mbusa Park anafotokoza chiombolo cha Ubatizo wa Yesu kwa iye.
Pa tsiku limenelo, mwamunayo anamva kwa nthawi yoyamba uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu Woyera ndipo anaomboledwa. Iye anamva uthenga wabwino kamodzi kokha ndipo anaomboledwa.
Uyo anali kafukufuku pa kusiya Ubatizo wa Yesu. Ife tinganene kuti ife tilibe uchimo koma ife ndithudi tidakali ndi uchimo m’mitima mwathu popanda Ubatizo wa Yesu. Anthu kawiri kawiri amanena kuti Yesu anayeretsa uchimo onse pokufa pa Mtanda, koma okhawo amene amakhulupilira mu Ubatizo ndi mwazi wa Yesu anganene kuti iwo alibe uchimo pamaso pa God. 
Mbusa Park anatsimikizira banja limeneli kuti ife sitingaomboledwe motheratu ku machimo athu popanda chiombolo kudzera mu Ubatizo wa Yesu. 
 
 

Chifaniziro cha Chipulumutso: Ubatizo wa Yesu 

 
Kodi chifaniziro cha chipulumutso ndi chiyani?
Ubatizo wa Yesu 
 
“Chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho Ubatizo.” Yesu anadza ku dziko lathu kuti atsuke machimo onse a dziko lapansi, kuti apange chikumbumtima chathu kukhala choyera ngati matalala Ife timayeretsedwa ku machimo onse chifukwa chakuti Yesu anatenga iwo onse pa Iye Mwini kudzera mu Ubatizo Wake. Iye anatipulumutsa ife ndi Ubatizo Wake ndi mwazi. Choncho, mtundu wonse wa anthu uyenera kugwada pamaso Pake. 
Ndife opulumutsidwa pokhulupilira mwa Yesu. Ife timakhala ana a God ndi kupita kumwamba pokhulupilira mwa Yesu. Ife timakhala olungama pokhulupilira mwa Yesu. Ndife ansembe achifumu. Ife tingatche God Atate wathu. Ife timakhala m’dziko lino lapansi, koma ndife mafumu.
Kodi inu mumakhulupiliradi kuti God anapulumutsa iwo a ife amene timakhulupilira m’madzi ndi Mzimu Woyera? Chiombolo chathu sichingakhale chokwanira popanda Ubatizo wa Yesu. Chikhulupiliro choona chimene God komanso Yesu amazindikira ndi kukhulupilira uthenga wabwino wa Yesu wotipulumutsa ife ndi Ubatizo Wake, Mtanda Wake, ndi Mzimu Woyera. Ichi ndiye chikhulupiliro chokha choona.
Machimo athu anatsukidwa pamene Yesu anatenga iwo ndi Ubatizo Wake ndipo machimo athu onse analipidwa pamene Iye anakhetsa mwazi pa Mtanda. Kristu Yesu anatipulumutsa ife ndi madzi ndi Mzimu Woyera. Inde! Ife timakhulupilira!
 
Ulaliki uwu ukupezekanso mu mtundu wa ebook. Dinani pachikuto cha buku pansipa.
KODI MWABADWADI MWATSOPANO MWA MADZI NDI MZIMU WOYERA? [Kusindikiza Kokonzedwanso Kwatsopano]