• All e-books and audiobooks on The New Life Mission website are free
  • Explore multilingual sermons in global languages
  • Two new revised editions in English have been released
  • Check out our website translated into 27 languages
Search

Sermons

Mutu 3: Uthenga Wabwino wa Madzi ndi Mzimu Woyera

[3-5] Tanthauzo la Uthenga Wabwino Woyamba wa Kubadwa Mwatsopano (Yohane 3:1-6)

Tanthauzo la Uthenga Wabwino Woyamba wa Kubadwa Mwatsopano(Yohane 3:1-6)
“Koma panali munthu wa Afarisi, dzina lace Nikodemo, mkulu wa Ayuda. Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa Iye, Rabi, tidziwa kuti inu ndinu mphunzitsi wocokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kucita zizindikilo zimene Inu mucita, ngati Mulungu sakhala naye. Yesu anayankha nati kwa iye, indetu, indetu, ndinena ndi iwe, ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona Ufumu wa Mulungu. Nikodemo ananena kwa Iye, munthu akhoza bwanji kubadwa atakalamba? Kodi akhoza kulowanso m’mimba ya amace ndi kubadwa? Yesu anayankha, indetu, indetu, ndinena ndi iwe, ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa Ufumu wa Mulungu. Cobadwa m’thupi cikhala thupi, ndipo cobadwa mwa Mzimu, cikhala Mzimu.” 
 
 

KODI TANTHAUZO LA KUBADWA MWATSOPANO NDI CHIANI MOGWIRIZANA NDI BAIBULO?

 
M’dzikoli, muli ambiri amene akufuna kubadwa mwatsopano pongokhulupilira mwa Yesu. Komabe, ndikufuna kukuuzani choyamba kuti kubadwa mwatsopano sikufuna kwathu, mwanjira ina, ndi chinthu chimene sichingabwere kudzera muzochita zathu zokha. 
 
Kodi kubadwa mwatsopano kumagwirizana ndi kutengeka kwa thupi ndi kusintha? 
Ai. Kubadwa mwatsopano kugwirizana ndi kusintha kwa mu uzimu. Ndi kwa ochimwa kuti abadwe mwatsopano ngati munthu opanda chimo.
 
Akristu ambiri ali ndi kusamvetsetsa kumeneku. Iwo akhulupilira kuti ali ndi chitsimikizo chobadwa mwatsopano. Amakhulupilira motero chifukwa cha zifukwa izi, mwa zina. Ena amayesa kuti ndi chipulumutso kumanga mipingo yambiri, ena amadzipereka okha m’kulalikira za Yesu ngati alaliki oyendayenda pakati pa anthu amene sanamvere mawu a Mulungu m’madera akumidzi, ndiponso, ena amakana kukwatiridwa ndi kutaya mphamvu zawo kuchita zimene akhulupilira kuti ndi nchito ya Mulungu. 
Izi sizonse. Palinso anthu ena amene amapereka ndalama zambirimbiri ku mpingo wawo, kapena mwina amasesa pansi pa mpingo wawo masiku onse. Mwazonsezi, amapereka nthawi yawo ndi katundu wawo ku mpingo. Ndipo akukhulupilira kuti mphamvu zonsezi zizawapindulitsa moyo waufumu. Amayembekezera kuti Mulungu adzazindikira mphamvu zawo ndi kuwalola iwo kubadwa mwatsopano. 
Mfundo ndi yakuti pali anthu ambiri odzipereka amene akufuna kubadwa mwatsopano. Amapezeka paliponse. Iwo amagwira nchito mwamphamvu, n’chiyembekezo chakuti tsiku lina Mulungu adzawadalitsa ndi kuwalola kubadwa mwatsopano. Iwo akupezeka pa mitundu yosiyanasiyana ya mabungwe a mpingo, m’masukulu, ndi mzipatala. Ndi tsoka kwambiri kuti sakudziwa choonadi cha kubadwanso mwatsopano. 
Onse amaganizira za m’khalidwe wa zochita zawo, “Ngati ndingachite ichi mwangwiro, ndizakhala obadwa mwatsopano.” Motero amaika mphamvu zawo zonse mu zinchito zimenezi, pakukhulupilira kuti akumanga maziko ofunikira kubadwa mwatsopano, ndi kuganiza kuti, “Inenso, ndizakhala obadwa mwatsopano tsiku lina, monga Mbusa Wesile!” Akawerenga Yohane 3:8, amasokoneza ndimeyi potanthauza kuti palibe anganene kumene madalitso a kubadwa mwatsopano amachokera kapena kumene akupita. 
Motero angazigwira nchito mwamphamvu kokha mwa chiyembekezo chakuti Yesu adzawalola kubadwa mwatsopano tsiku lina. Pali ambiri amene akuganiza kuti, “Ngati ndikupitiliza kuyesayesa motere, Yesu adzandilola kubadwa mwatsopano tsiku lina. Ndizakhala obadwa mwatsopano kopanda ngakhale kudziwa za zimenezi. M’mawa mwina ndizadzuka ndili obadwa mwatsopano ndipo ndizadziwa kuti ndine oyenerera Kumwamba.” Ndi chiyembezezo ndi chikhulupiliro chotani chopanda zipatso chimenechi! 
Sitingakhale obadwa mwatsopano m’njira imeneyo! Sitingakhale obadwa mwatsopano mwa kusiya kumwa mowa kapena kusuta fodya, kapena kupezeka pa mpingo molimbikira. Monga m’mene Yesu ananenera, tiyenera “kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu” kuti tilowe mu Ufumu wa Mulungu. Ndipo madzi ndi Mzimu ndiye zilolezo za Mulungu zokha za kubadwanso mwatsopano. 
Ngati munthu sabadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu, mphamvu zake zofuna kukhala olungama pamaso pa Yesu ndi zachabe. Munthu sangabadwe mwatsopano ndi zopereka, misonkho, kapena kuzipereka. Munthu angaganize kuti chifukwa Mulungu Yekha ndiye akudziwa amene ali obadwa mwatsopano, iye sangadziwe ngati ndi obadwa mwatsopano kapena ai. 
Kungakhale kotsitsimula kuganiza m’njira imeneyo, koma kubadwa mwatsopano sikungabisike kunsi kwa thebulo. Munthu ayenera kuziwa yekha, ndipo ena angamve. 
Mwina sitingathe kumvera mwakuthupi, koma tingamvere bwinobwino mwakuuzimu. Obadwa mwatsopano oona ndi okhulupilira mkubadwanso kudzera m’mawu a Mulungu, mawu a madzi, mwazi ndi Mzimu. Komabe, iwo amene sanabadwe mwatsopano sangamvetsetse monga m’mene Nikodemo analili. 
Motero tiyenera kumvera ku mawu a choonadi, chiombolo kudzera mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Pamene tikumvera ndi kuphunzira mawu a Mulungu, tingapeze choonadi m’menemo. Motero ndi kofunika kwambiri kutsegula maganizo athu ndi kumvetsera mwatcheru. 
“Mphepo iomba pomwe ifuna, ndipo ukumva mau ace, koma sudziwa kumene icokera, ndi kumene imuka; cotero ali yense wobadwa mwa Mzimu” (Yohane 3:8).
Pamene munthu amene sanabadwe mwatsopano awerenga ndime imeneyi, amaganiza kuti, “Aha, Yesu ananena kuti sindingadziwe ndiliti pamene ndingabadwe mwatsopano! Palibe yemwe akudziwa!” Ndipo maganizo amamptsa chitsitsimutso. Koma ichi sichoona. Sitingadziwe kumene mphepo ukuchokera kapena kumene ukupita, koma Mulungu akudziwa zonse.
Ngakhale pakati pa obadwa mwatsopano, pali ena amene sanazindikire izi pa chiyambi. Ichi ndi chomveka. Koma mkati mwa mtima wa munthu ameneyu, muli Uthenga Wabwino; mawu achiombolo kudzera mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu. 
Uwu ndi umboni wakubadwanso mwatsopano. Iwo amene akumvera uthenga adzazindikira ndi kunena kuti, “Oho, ndiye kuti ndilibe uchimo. Ndiyeno, ndapulumutsidwa ndipo ndine obadwa mwatsopano.” Pamene akhulupilira ndi kusunga Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu mu mtima wawo, amakhala olungama, ana a Mulungu. 
Wina angafunsidwe, “Kodi ndinu obadwanso mwatsopano?” ndipo angayankhe, “Ndikalibe.” “Ndiyeno, kodi ndinu opulumutsidwa?” “Inde, ndikhulupilira kuti ndine opulumutsidwa.” Koma akupanga ndemanga yachikaikitso, kodi sakutero? Iye akutero chifukwa akuganiza kuti pamene munthu wabadwa mwatsopano, ayenera kusinthidwanso kuthupi lake. 
Anthu otere amaona kubadwa mwatsopano ngati chinthu china chosinthidwa mu umoyo. Koma choonadi ndi chakuti sakumvetsa uthenga wakubadwanso mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. 
Pali ambiri amene sakumvetsetsa tanthauzo la kubadwanso mwatsopano. Ndi chachisoni kwambiri. Si anthu wamba okha, komanso azitsogoleri ambiri mu mpingo amene akugwira nchito pansi pa chithunzi chimenechi. Mitima ya ena a ife amene ndi obadwa mwatsopano ikulilira anthu amenewa. 
Ngati tikumvera m’njira imeneyi, kodi ndi chowawa chotani chimene chikupweteka Yesu Mulungu wathu Kumwamba? Tiyeni tonse tibadwenso mwatsopano mwa kukhulupilira mu uthenga wa kubadwanso mwatsopano mwa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake a pa Mtanda. 
Kubadwa mwatsopano ndi kukhala opulumutsidwa kukutanthauza chinthu chimodzi. Komabe, pali ambiri amene sakudziwa choonadi chimenechi. Kubadwa mwatsopano kukutanthauza kuti uchimo mu mtima wathu unatsukidwa kudzera mu kukhulupilira mu Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu. Chikutanthauza kukhala olungama kudzera mu chikhulupiliro cha mu ubatizo wa Yesu ndi nsembe Yake ya pa Mtanda. 
Asanabadwe mwatsopano, anthu ndi ochimwa, koma pambuyo pake, anakhala alibiretu uchimo konse, obadwanso mwatsopano ngati munthu watsopano. Iwo anakhala ana a Mulungu mwa kukhulupilira mu Uthenga Wabwino wa chipulumutso. 
Kubadwa mwatsopano kukutanthauza kuvala zovala za ubatizo wa Yesu, kufa pa Mtanda limodzi ndi Iye, ndi kuuka nayenso limodzi. Zikutanthauza kuti munthu wakhala olungama kudzera mu mau a ubatizo ndi Mtanda wa Yesu. 
Pamene munthu wabadwa m’mimba mwa mai, iye ndi ochimwa. Koma ngati wamvera uthenga oona wa kubadwanso mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu, iye amabadwanso mwatsopano ndipo amakhala olungama. 
Kunja munthu otere amaoneka osasiyana, koma ndi obadwanso mwatsopano mkati, mu mzimu. Ichi ndi chimene chikutanthauza pa za kubadwanso mwatsopano. Koma pali ochepa kwambiri amene akudziwa choonadi; osati ngakhale m’modzi pa zikwi khumi. Kodi mungagwirizane nane kuti pali ochepa amene akumvetsetsa tanthauzo loona la kubadwanso mwatsopano? 
Iwo amene akukhulupilira mu Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu ndipo abadwanso mwatsopano angasiyanitse kubadwanso mwatsopano koona ndi Akristu wamba. 
 

NDI YESU AMENE AKULAMULIRA MPHEPO 

Ndani angadziwe amene anapulumutsidwa?
Okhao obadwanso mwatsopano 
 
“Mphepo iomba pomwe ifuna, ndipo ukumva mau ace, koma sudziwa kumene icokera, ndi kumene imuka; cotero ali yense wobadwa mwa Mzimu.” Yesu anali kunena za iwo amene sanabadwe mwatsopano. Obadwa mwatsopano akudziwa za kubadwa mwatsopano, koma Nikodemo sankadziwa. Mulungu akudziwa amene ali obadwa mwatsopano, ndipo obadwa mwatsopano naonso akudziwa chimenechi. 
Komabe, iwo amene sanabadwe mwatsopano sakudziwa m’mene munthu ayenera kubadwira mwatsopano monga m’mene sakudziwira kumene mphepo ikuchokera ndi kumene ikupita. 
Kodi mukutha kumvetsa chimenechi? Kodi ndani akuyendetsa mphepo? Mulungu. Ndindani analenga mphepo? Analenga ndi Mulungu kumwamba. Ndani amasintha nyengo padziko lapansi, kupanga njira ya mphepo ndi madzi? Ndipo ndani anaika mpweya wa moyo mu zinthu zonse za moyo? M’mawu ena, ndani analenga zamoyo zonse m’dzikoli ndi kuzipanga kuti zichuluke? Palibenso wina koma Yesu Kristu. Ndipo Yesu ndi Mulungu. 
Pamene sitikudziwa mawu a Uthenga Wabwino wa madzi,mwazi ndi Mzimu, sitingabadwenso mwatsopano ndipo sitingaphunzitsenso ena mwauzimu. Yesu anatiuza kuti ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, munthuyo sangabadwe mwatsopano. 
Tiyenera kukhulupilira mu Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu, uthenga wamphamvu umene upangitsa ife kubadwanso mwatsopano. Mzimu umalowa ndi kukhala m’mitima mwa onse amene akhulupilira mu uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu. 
Yesu Kristu anabatizidwa kuti achotse machimo onse a mtundu wa anthu, ndipo anakhetsa mwazi pa Mtanda kuti alipire machimo amenewa. Iye anaika chipulumutso cha kubadwa mwatsopano m’mitima ya mtundu wa anthu onse. Pamene tikukhulupilira mu uthenga umenewu, Mzimu umalowa moyo wathu. Ichi ndi chipulumutso cha kubadwa mwatsopano. Pamene tikukhulupilira mu kutsuka kwa machimo onse kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, ndifedi obadwa mwatsopano. 
 Mu Genesis 1:2, munalembedwa kuti, “Dziko lapansi ndipo linali lopanda kanthu; ndipo mdima unali pamwamba pa Nyanja; ndipo Mzimu wa Mulungu unalinkufungatira pamwamba pa madzi.” Munalembedwa kuti Mzimu wa Mulungu unali kunfungatira pamwamba pa madzi. Mzimu wa Mulungu unali kuyendayenda pamwamba pa dziko lapansi. 
Kutanthauza kuti Mzimu sungalowe mu mitima ya ochimwa. Mtimwa munthu amene ndi osabadwa mwatsopano uli m’zowawa, uli odzala ndi mdima wa uchimo. Motero Mzimu wa Mulungu sungathe kulowa mu mtima mwa munthu otere. 
Mulungu anatumiza kuunika kwa uthenga Wake Wabwino kuti kuunikire m’mitima ya ochimwa. Mulungu anati, “Kuyere” (Genesis 1:3), ndipo kuwala kunakhalako. Ndiyeno, pokhapo, mpomwe Mzimu wa Mulungu ungakhale m’mitima ya anthu onse. 
Motero, m’mitima ya obadwa mwatsopano, iwo amene akhulupilira mu uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu, mukhala Mzimu wa Mulungu. Ilo ndiye tanthauzo la kukhala “obadwa mwatsopano.” Iwo ndi obadwa mwatsopano m’mitima yawo chifukwa anamvera ku mawu a chipulumutso cha madzi ndi Mzimu ndipo anawakhulupilira! 
Kodi munthu angakhale bwanji obadwa mwatsopano? Yesu anafotokozera Nikodemo, M’falisi, kuti, “Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa Ufumu wa Mulungu.” Nikodemo anati, “Kodi tingakhale motani obadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu? Kodi tingalowenso m’mimba mwa amai athu kachiwiri ndi kubadwanso mwatsopano?” Mwachionekere, iye anaziona mosadziwa ndipo sanadziwe m’mene munthu ayenera kukhalira obadwa mwatsopano. 
Yesu anati kwa iye, “Ndiwe M’phunzitsi, ndipo sukudziwa chimene chikutanthauza?” Yesu anamuuza kuti ngati munthu sakhala obadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu, sangalowe mu Ufumu wa Kumwamba kapena ngakhale kuuona. Yesu anauza Nikodemo choonadi cha kubadwa mwatsopano. 
Ndi zoona kuti kuli anthu ambiri amene akukhulupilira mwa Yesu kopanda kubadwa mwatsopano. Akristu ambiri ali ngati Nikodemo osabadwa mwatsopano. 
Nikodemo anali mtsogoleri wauzimu wa Israeli nthawi imeneyo, chimodzimodzi monga atsogoleri a mpingo masiku ano. Mu nthawi zino, iye anali kulinganizidwa ndi wampando wamkulu. Mwa kapimidwe ka chipembezo iye anali m’phunzitsi, mphunzitsi wa Ahebri, Iye anali mtsogoleri wa chipembezo cha Ayuda. Iye anali M’yuda. Iye analinso ophunzira womaliza. 
Mu Israeli masiku amenewo, kunalibe mabungwe omwe mungasiyanitse ndi masukulu a masiku ano, choncho anthu onse anali kupita ku kachisi kapena ku masunagoge kukaphunzira pansi pa “anthu ophunzira.” Iwo anali aphunzitsi a anthu. Monga m’mene zilili lero, kulinso aziphunzitsi abodza ambiri m’nthawiyo. Ndipo anali kuphunzitsa anthu kopanda kubadwa mwatsopano iwo okha. 
Masiku ano kuli atsogoleri amipimgo ambiri, akuluakulu a mpingo, aziphunzitsi, alaliki, akulu ndi ma dikoni, amene sanabadwe mwatsopano. Monga Nikodemo, iwo sakudziwa choonadi cha kubadwa mwatsopano. Ambiri amaganiza kuti tiyenera kulowa m’mimba mwa mai kachiwiri kuti tibadwenso mwatsopano. Iwo akudziwa kuti ayenera kubadwanso mwatsopano koma sakudziwe m’mene ayenera kuchitira. 
Ndipo chifukwa cha umbuli wawo, monga munthu wakhungu akugwira njobvu kuyesa mwachabe kusiyanitsa ndi manja awo okha, malangizo awo akuchokera ku m’mene akumverera ndi ukatswiri wao. Iwo amalalikira zinthu za kudziko mu mpingo. Chifukwa cha ichi, akristu okhulupirika ambiri akuletsedwa kubadwa mwatsopano. 
Kubadwa mwatsopano sikugwirizana ndi zochita zathu zabwino. Ndife obadwa mwatsopano kudzera m’chikhulupiliro cha mawu a madzi , mwazi ndi Mzimu umene Mulungu anapereka kwa ife. Ndi uthenga wabwino wa Mulungu umene unasintha ife kuchoka mu kukhala ochimwa kupita mu kukhala olungama. 
Yesu ananena mawu amenewa, “Ngati ndakuuzani za pansi pano, ndipo simukhulupira, mudzakhulupira bwanji, ngati ndikuuzani za Kumwamba?” (Yohane 3:12) Indedi, anthu sanakhulupilire pamene Yesu anawauza choonadi chakuti chitetezero cha machimo athu onse chinatsirizika kudzera mu ubatizo Wake. Kodi iwo ndi chiani chimene sanakhulupilire? Iwo sanakhulupilire kuti chiombolo chawo chinatheka kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi imfa Yake ya pa Mtanda. Ichi ndi chimene Iye anatanthauza pamene ananena kuti anthu sangakhulupilire mwa Iye ngati angawauze za “zinthu za Kumwamba.” 
Kuti atiyeretse ku machimo athu onse, Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi ndi kufa pa Mtanda, ndiyeno anaukitsidwa kwa akufa kuti akonze njira ya Ochimwa kuti abadwe mwatsopano. 
Motero Yesu anafotokozera Nikodemo mwa kugwira mawu a mu Chipangano Chakale. “Ndipo kulibe munthu anakwera Kumwamba, koma Iye wotsikayo kucokera Kumwamba, ndiye Mwana wa munthu, wokhala m’Mwambayo. Ndipo monga Mose anakweza njoka m’cipululu, cotero Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa; kuti yense wakukhulupira akhale nao moyo wosatha mwa Iye” (Yohane 3:13-15). Monga Mose anakwezera njoka m’mwamba m’chipululu, Momwemonso Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa m’mwamba kuti alole aliyense okhulupilira mwa Iye akhale nawo moyo osatha. 
Kodi Yesu anatanthauzanji pamene ananena kuti, “Ndipo monga Mose anakweza njoka m’cipululu, cotero Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa?” (Yohane 3:14) Iye anagwira ndime imeneyi kuchokera mu Chipangano Chakale kuti afotokoze m’mene ubatizo Wake ndi mwazi uzabweretsera chitetezero cha machimo onse a mtundu wa anthu. 
Kuti Yesu afe pa Mtanda, kuti Iye akwedzedwe, anayamba wachotsa uchimo wa dziko mwa kubatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Chifukwa Yesu analibe uchimo, sakanapachikidwa pa Mtanda. Kuti Iye apachikidwe pa Mtanda, anayenera kubatizidwa ndi Yohane Mbatizi ndipo motero anyamule machimo onse a dziko pa Iyeyekha. 
Mwa kunyamula kokha machimo athu ndi kulipira ndi mwazi Ake, ndi pomwe akanapulumutsa ochimwa onse ku chionongeko. Yesu anatipatsa chipulumutso cha kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. 
Motero iwo amene akhulupilira mwa Yesu ngati Mpulumutsi wawo amavala zovala za ubatizo Wake, kufa limodzi Naye, ndipo ndi kubadwa mwatsopano limodzi Naye. Patsogolo pake, Nikodemo anadza kuzamvetsetsa chimenechi. 
 
 
MONGA NJOKA INAKWEZEDWA M’MWAMBA 
 
N’chifukwa chiani Yesu anapachikidwa? 
Chifukwa chakuti anachotsa uchimo onse kudzera mu ubatizo Wake.
 
Kodi mudziwa nkhani ya m’mene Mose anakwezera njoka yamkuwa m’chipululu? Nkhaniyi inalembedwa mu Numeri 21. Ikunena kuti miyoyo ya Israyeli inakhala yovuta atachotsedwa ku Iguputo, kupangitsa kuti aziyankhula zotsutsana Mulungu komanso Mose. 
Mwa ichi, Ambuye anatuma njoka yoopsa pakati pa anthu, imene inalowa m’makhumbi awo ndi kuwaluma ndi kuwapha. Atalumidwa, matupi awo anayamba kuonongeka ndipo ambiri anafa. 
Pamene anthu anayamba kufa, Mose, mtsogoleri wawo, anapemphera kwa Mulungu. “Ambuye, chonde tipulumutseni.” Mulungu anamuuza kuti apange njoka yoopsa yokhala ndi mkuwa ndi kuiika pa mtengo. Iye anamuuza kuti aliyense amene adzayang’ana njokayo adzakhala ndi moyo. Mose anachita m’mene anamuuzira ndi kuuza anthu mawu a Mulungu. 
Aliyense amene anakhulupilira m’mawu ake ndi kuyang’ana kwa njoka yamkuwa anachilitsidwa. Mwa njira imeneyi, tiyenera kuchiritsidwa ku kalumidwe ka poizoni wa mdierekezi. Anthu a ku Israeli anamvera kwa Mose ndi kuyang’ana kwa njoka yamkuwa pa mtengo, ndipo motero anachiritsidwa. 
Chibvumbulutso cha njoka pa mtengo chinali chakuti chiweruzo cha machimo a mtundu onse wa anthu chinabwera pa Yesu Kristu kudzera mu ubatizo Wake ndi imfa pa Mtanda. Iye anadzitengera Yekha kuti alipire chilango cha machimo onse a ochimwa m’dziko. Motero, anamaliza chilango chonse cha machimo athu. 
Yesu anabwera m’dzikoli kuzapulumutsa anthu onse, amene anayenera kufa ku “poizoni ya njoka,” chiyeso cha Satana. Kuti alipire machimo athu onse, Anayenera kubatizidwa ndi kufa pa Mtanda asanaukitsidwe kuti apulumutse iwo amene akhulupilira mwa Iye. 
Monga Israyeli mu Chipangano Chakale anachilitsidwa pamene anayang’ana njoka pamwamba pa mtengo, lero onse amene akhulupilira mwa Yesu ndipo ali ndi chikhulupiliro chakuti Iye analipira machimo athu kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi angapulumutsidwe ndi kubadwa mwatsopano. 
Yesu analipira mwanthunthu machimo onse a dziko kudzera mu ubatizo Wake ndi Yohane M’batizi pa Yordano, imfa Yake pa Mtanda, ndiponso kuukitsidwa Kwake kwa akufa. Tsopano, onse amene akhulupilira mwa Iye angadalitsidwe ndi chipulumutso kudzera m’chifundo Chake. 
“Ndipo kulibe munthu anakwera Kumwamba, koma Iye wotsikayo kucokera Kumwamba, ndiye Mwana wa munthu, wokhala m’Mwambayo.” (Yohane 3:13). Mwa malipiro a machimo athu, Yesu anabatizidwa ndi kukhetsa mwazi pa Mtanda ndi kutsegula chipata cha Kumwamba kwa ife. “Ine ndine njira, ndi coonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine,” anatero Yesu mu Yohane 14:6. 
Chifukwa chakuti Yesu anabatizidwa ndi kupachikidwa pa Mtanda kuti atsegule zipata za Kumwamba za ife, tonse amene tikhulupilira m’chipulumutso kudzera mwa Iye tinapulumutsidwa. Yesu analipira kale machimo athu, choncho aliyense amene akhulupilira mu choonadi cha madzi, mwazi ndi Mzimu angalowe mu Ufumu wa Kumwamba. 
Yesu anatipulumutsa ife ndi uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Kubadwa mwatsopano kuchokera mkukhala ndi chikhulupiliro mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu ndiponso muchoona chakuti Iye ndi Mulungu. 
“Ndipo monga Mose anakweza njoka m’cipululu, cotero Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa;” (Yohane 3:14). Kodi ndime imeneyi ikutanthauza chiani? Kodi nchifukwa chiyani Yesu anayenera kupachikidwa? Kodi Iye anachita chimo monga ife? Kodi anali ofoka monga ife? Kodi Iye anali operewera monga ife? Ai, Iye sanali choncho. 
Ndiyeno, Kodi n’chifukwa chiani anayenera kupachikidwa? Kunali kwakuti apulumutse ife ndi kulipira machimo athu onse. Iye anabatizidwa ndi kupachikidwa kuti apulumutse onse a ife ku machimo athu onse. 
Ichi ndi choonadi cha chipulumutso, cha kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Yesu anapereka moyo watsopano kwa onse amene akhulupilira mu ubatizo Wake ndi imfa Yake ya pa Mtanda, imene inali malipiro ya machimo athu. 
 
 

TANTHAUZO LA MADZI NDI MZIMU 

 
Kodi chikutanthauzanji Mwa madzi ndi Mzimu? 
Madzi akutanthauza ubatizo wa Yesu ndipo Mzimu akutanthauza Iye kukhala Mulungu.
 
Baibulo likutiuza kuti pamene tikukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake pa Mtanda, ndiye kuti ndife obadwa mwatsopano. Kukhala ana a Mulungu, kubadwa mwatsopano, kukwaniritsidwa mwa mawu olembedwa a Mulungu, uthenga wabwino wa madzi, mwazi ndi Mzimu umene ndi malipiro a machimo athu. 
Mogwirizana ndi Baibulo, “madzi” akutanthauza ubatizo wa Yesu (1 Petro 3:21), ndipo “Mzimu” akutanthauza kuti Yesu ndi Mulungu. Ndipo ichi ndi choonadi cha kubadwa mwatsopano, kuti Yesu anadza padzikoli mwa thupi la mtundu wa anthu kuti alipire machimo athu kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi. 
Iye anachotsa machimo athu onse kudzera mu ubatizo Wake ndi kulipira mphotho ya uchimo mwa kufa pa Mtanda. Mwa kubatizidwa ndi kukhetsa mwazi pa Mtanda, anapulumutsa onse amene akhulupilira mwa Iye. 
Tiyenera kuzindikira kuti ubatizo ndi mwazi wa Yesu akuimira chipulumutso chathu mwakuti anatipulumutsa ku machimo athu. Okhawo amene anabadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu ndi amene angaone ndi kulowa mu Ufumu wa Kumwamba. Yesu anapulumutsa ife ndi madzi a ubatizo Wake, mwazi Ake ndi Mzimu. Kodi mumakhulupilira mu zimenezi? 
Yesu ndi Wamkulu Wansembe wa kumwamba amene anadza kudzikoli kuzalipira machimo a dziko. Iye anabatizidwa, kukhetsa mwazi pa Mtanda ndipo anaukitsidwa, motero anakhala Mpulumutsi wa onse amene akhulupilira mwa Iye. 
Yesu anati mu Yohane 10:7, “Ine ndine khomo la nkhosa.” Yesu waima pakhomo la kumwamba. Ndani akutitsegulila khomo? Ndi Yesu Kristu. 
Iye amatembenuza nkhope Yake kwa iwo amene akhulupilira mwa Iye kopanda kudziwa choonadi cha chipulumutso Chake. Iye salola iwo amene sakhulupilira mu ubatizo Wake, mwazi ndi Mzimu kubadwa mwatsopano. Iye amatembenuza nkhope Yake kwa aliyense amene sakhulupilira mu mawu Ake olembedwa, amene akukana kuvomereza kuyera Kwake, ndiponso iye amene sakuzindikira Iye kukhala Mulungu. 
Choonadi cholembedwa ndi chakuti anabwera kudzikoli m’thupi, anabatizidwa, ndi kufa pa Mtanda kuti alipire machimo onse a dziko, kuti anafa pa Mtanda kuti alandire chiweruzo m’malo mwathu, kuti anaukitsidwa pa tsiku la chitatu pambuyo pa kupachikidwa Kwake. Aliyense akukana kukhulupilira mu choonadi chimenechi amachotsedwa ndi Iye ndipo adzaonongedwa. Monga kunalembedwera, “mphotho yace ya uchimo ndi imfa” (Aroma 6:23).
Iwo komabe, amene akhulupilira m’dalitso la chiombolo kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi, iwo amene anakhala oyera m’mitima yawo, ndi wovomerezedwa kulowa mu Ufumu wa Kumwamba. Uwu ndi uthenga wabwino oona wa kubadwa mwatsopano, uthenga wabwino umene unabwera kwa ife mwa madzi, mwazi ndi Mzimu. Kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu ndi uthenga wabwino wakumwamba. Okhawo amene akhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu ndi amene angathe kubadwa mwatsopano. Iwo amene akhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi, mwazi ndi Mzimu ndi amene alibe uchimo; ndi amene ali obadwadi mwatsopano. 
Lero, monga Nikodemo yemwe sankadziwa choonadi, anthu ambiri akukhulupilira mwa Yesu kopanda kudziwa uthenga wabwino oona. Anali membala wapamwamba chotani Nikodemo m’gulu lake! Komabe, iye anamvera uthenga wabwino oona kwa Yesu, ndipo patsogolo pake, pamene Yesu anali kupachikidwa, anali m’modzi yemwe anaika thupi Lake. Pa nthawi imeneyo Nikodemo anali okhulupirika mwanthunthu. 
Masiku ano, pali ambiri a ife amene sitikudziwa choonadi cha madzi ndi Mzimu wa Yesu. Kuonjezerapo, palinso anthu ambiri amane sakuvomereza choonadi pamene ali ndi mpata wakumva uthenga wabwino oona. Ndi zachisoni kwambiri. 
Yesu anakwanitsa kuti ife tonse tikhale obadwa mwatsopano. Kodi n’chiani chinatipanga ife kubadwa mwatsopano? Anali madzi, mwazi, ndi Mzimu. Yesu anachotsa machimo athu pamene anabatizidwa. Iye anafa pa Mtanda ndipo ndiyeno anaukitsidwanso kwa akufa. 
Ndipo amapereka zonse kwa iwo amene akhulupilira mwa Iye daliso la kubadwa mwatsopano. Yesu ndi Mpulumutsi amene akulola iwo onse amene akhulupilira mwa Iye kubadwa mwatsopano. Pempherani kuti nthawi zonse muzikhala ndi Yesu, amene analenga Kumwamba ndi dziko lapansi ndi zinthu zonse za m’menemo. 
Yohane 3:16 anena, “kuti yense wakukhulupilira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha” Tinapeza moyo osatha mwa kukhulupilira mwa Yesu. Tabadwa mwatsopano pokhulupilira mu madzi ndi Mzimu. Ndi choonadi chimene ngati tikhulupilira mu uthenga wa chipulumutso, ubatizo ndi mwazi wa Yesu, ndiponso kuti Yesu ndi Mpulumutsi komanso Mulungu, tingapulumutsidwe. 
Koma ngati sitikhulupilira mu choonadi chimenechi, tidzaponyedwa mu gehena kwamuyaya. Ndi chifukwa chake Yesu anauza Nikodemo, “ngati ndakuuzani za pansi, ndipo simukhulupira, mudzakhulupira bwanji, ngati ndikuuzani za Kumwamba?” 
Kodi Mulungu anachita chiani kwa ife? Chipulumutso kudzera mwa Yesu chinatilola kubadwa mwatsopano. Yesu anatipulumutsa ku dziko, mdierekezi ndi kumachimo a dziko. Kuti apulumutse ochimwa a kudzikoli kuchiweruzo cha uchimo, Iye anachotsa machimo athu onse kudzera mu ubatizo Wake, anapachikidwa pa Mtanda ndiponso anaukitsidwanso kwa akufa. 
Ndi chisankho chathu kuti mwina tikhulupilire m’chipulumutsochi kapena ai. Chipulumutso cha kubadwa mwatsopano chichokera mu kukhulupilira m’chipulumutso kudzera mu ubatizo ndi mwazi a Yesu. 
Kunanenedwa kuti kuli madalitso awiri amene Mulungu anaika pa ife. Limodzi ndi dalitso laonse, limene likuphatikizapo zinthu zonse zachilengedwe, kuphatikizanso dzuwa ndi mphepo. Ili likutchedwa dalitso laonse chifukwa linaperekedwa kwa anthu onse ochimwa kapena olungama. 
Ndiyeno, kodi dalitso lapadera limeneli ndi lotani? Dalitso lapadera ndi kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu, amene anapulumutsa ochimwa onse ku imfa chifukwa cha machimo awo. 
 

DALISO LAPADERA
 
Kodi dalitso lapadera ndi chiani? 
Kubadwa mwatsopano kudzera mu ubatizo wa Yesu, kupachikidwa Kwake ndi kuukanso Kwake.
 
Munalembedwa mu Yohane 3:16, “Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wace wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupilira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.” Ichi chikusonyeza dalitso lapadera la Mulungu: Yesu anadza kudzikoli kuthupi la munthu ndi kutsuka machimo athu onse mwa kubatizidwa ndi kupachikidwa chifukwa cha ife. Ili ndi dalitso lapadera la Mulungu, choonadi, chimene chinatipulumutsa ku machimo onse. 
Ndi choona chakuti Yesu anapulumutsa ife ndi kutisintha kuchoka pa ochimwa kukhala olungama. Mungakhale ndi dalitso lapadera la Mulungu mosavuta mwa kukhulupilira mu choonadi chimenechi. Kodi inu nonse mukukhulupilira? 
Chikhulupiliro chanu chonse chidzakhala chachabe ngati mukukana dalitso lapadera la Mulungu zilibe kanthu kuti mwakhala okhulupirika pa umoyo wanu onse. 
Ndikulalikira nthawi zonse ndi ndipo sindinaiwalepo kulalikira kuti kukhulupirira mu ubatizo wa Yesu ndi Mtanda Wake ndi njira yokha yokhalira obadwa mwatsopano. Buku lililonse la m’Baibulo likuvumbulutsa kuti dalitso la kubadwa mwatsopano kudzera mwa Yesu ndi “dalitso lapadera la Mulungu” limene tikunena. Palibe chimene chikufotokoza bwino za dalitso la Mulungu koposa chipulumutso cha ochimwa kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi kupachikidwa Kwake. 
Ubatizo wa Yesu ndi kupachikidwa Kwake ndi madalitso a Mulungu. Alaliki abodza a m’dzikoli alibe chonena pa chimenechi. Awa alaliki abodza amaoneka m’zovala za angelo a kuwala, ali ndi makhalidwe a chiKristu ndi umunthu. Inde, Izi ndi zoona. Zodabwitsa zimene akuchita, kuchilitsa odwala zonse ndi zoipa ngati alibe chochita ndi dalitso lapadera la Mulungu. 
Ndi dalitso lapaderali la Mulungu limene linapatsa ife ochimwa uthenga wabwino wa chitetezero cha machimo. Ndi dalitso lake lapaderali, Mulungu analola ife kubadwanso mwatsopano. Iye anatipanga ife atsopano kudzera mu ubatizo Wake, mwazi, imfa ndi kuukanso. Iye anatipanga ife ana Ake, kumasuka ku uchimo. 
Kodi mumakhulupilira mu zimenezi? ― Inde. ― Kodi munadalitsidwadi moona? ― Inde. ― Ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake, imfa ndi kuuka Kwake ndi madalitso apadera amene Mulungu anapereka kwa ife kudzera mwa madzi ndi Mzimu. Uwu ndi uthenga wabwino wa dalitso lapadera. Tamandani Ambuye chifukwa cha kutipulumutsa kudzera mu dalitso Lake lapadera 
Ndi zachisoni kuti aKristu ambiri okhulupirika lero sakudziwa za madalitso apadera a Mulungu, uthenga wabwino wa ubatizo ndi mwazi, wakubadwanso mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Amayesera mwakhungu kupeza njira mu maphunziro awo a za umulungu ndi khalidwe la chipembezo. Ali mbuli chotani amenewa! 
ChiKristu chakhala ndi ife kwa nthawi yaitali. Papita zaka pafupifupi mazana asanu kuyambira pa Kukonzanso. Koma ngakhale ndi chonchi, pali ambiri ku Korea ndiponso padziko lonse lapansi amene ali mbuli za choonadi cha kubadwa mwatsopano ndi dalitso lapadera la Mulungu. 
Ndili ndi chiyembekezo, komabe, ndi kukhulupilira kuti Iye adzawadziwitsa choonadi chifukwa tili mu nthawi imene ili kufupi ndi kutha kwa dzikoli. 
Ochimwa ayenera kubadwanso mwatsopano ndi kuvomereza choonadi cha madzi ndi Mzimu kuti akhale olungama ndi kulowa mu Ufumu wa Kumwamba. AKristu ambiri akuyesera kubadwa mwatsopano. 
Komabe, ngati akuyesa kopanda kudziwa tanthauzo loona la kubadwa mwatsopano, chikhulupiliro chawo chili mwachabe. Iwo amanena kuti ayenera kubadwanso mwatsopano kuti alowe mu Ufumu wa Kumwamba, Koma sakudziwa chilichonse cha choonadi cha kubadwa mwatsopano. 
Amangoganizira kuti pakuti akukhulupilira mwa chikhulupiliro chonse ndi kumvera moto m’mitima yawo, angakhale obadwa mwatsopano. Koma kuyesa kubadwa mwatsopano kuchokera m’mene munthu akumverera kapena zofunika zimene zipembedzo zikuchita zingakutsogolereni kokha ku chikhulupiliro cholakwika. 
 
 

MAWU A MULUNGU AMENE AKUTSOGOLERA IFE KUTI TIKHALE OBADWADI MWATSOPANO

 
Kodi kusiyana kuli pati pakati pa chikhulupiliro ndi chipembezo?
Chikhulupliro ndi kukhulupilira zimene Yesu anachita kuti apulumutse ife, pamene chipembezo ndi kudalira pa maganizo a munthu ndi zinchito.
 
Munalembedwa poyera mu 1 Yohane 5:4-8 kuti tingakhale obadwa mwatsopano pongokhulupilira m’madzi, mwazi ndi Mzimu. Ngati tingakhale obadwa mwatsopano, tiyenera kusunga m’maganizo kuti tingakhale obadwa mwatsopano kokha kudzera m’mawu olembedwa a Mulungu, mawu a choonadi. Tiyenera kudziwa kuti masomphenya, kuyankhula m’malilime kapena m’nzeru zodabwitsa sizingatitsogolerere mu kubadwa mwatsopano. 
Yesu anati mu Yohane 3 kuti munthu sangalowe mu Ufumu wa Kumwamba ngati sanabadwe mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Ngati munthu akafuna kubadwa mwatsopano, Iye ayenera kukhulupilira mwa Yesu kawiri. Choyamba, iye amakhulupilira mwa Yesu m’njira ya kupembeza, azindikire machimo ake kudzera mu lamulo la Mulungu. Nthawi yoyamba imene munthu wakhulupilira mwa Yesu, ndi kudzera mwa lamulo la Mulungu kuti azindikire m’mene alili ochimwa. 
Sitiyenera kukhulupilira mwa Yesu mogwirizana ndi chimodzi mwa zipembezo za m’dziko. ChiKristu sichipembezo chokha. Ndi njira yokha yopezera moyo wosatha kudzera m’chikhulupiliro. 
Aliyense amene wakhulupilira mwa Yesu ngati chipembezo adzakhala opanda kanthu. Adzasiidwa ali ndi mtima odzala ndi uchimo, zowawa ndi kupanda kanthu. Kodi ichi sichoona? Simuyenera kukhala wachinyengo monga analili Afalisi mu Baibulo. 
Aliyense akufuna kukhala mKristu-obadwa mwatsopano. Komabe, pamene munthu akukhulupilira mu chiKristu ngati chipembezo, adzakhala wachinyengo ndi mtima odzala ndi uchimo. Tiyenera kukhala odziwa choonadi cha kubadwa mwatsopano. 
Aliyense amene akhulupilira m’chiKristu ngati chipembezo popanda kubadwa mwatsopano ali oyenera kukhala ndi chisokonezo komanso kupanda kanthu mu mtima wake. Ngati munthu akhulupilira mwa Yesu koma sanabadwe mwatsopano, chikhulupiliro chake ndi cholakwika. Motero adzakhala ngati wachinyengo, akuyesa kwambiri kuoneka oyera pamaso pa aliyense koma kugwa mochititsa manyazi. 
 Ngati mukhulupilira m’chiKristu ngati chipembezo, mudzakhalabe ochimwa, wachinyengo, ndi kukhala m’masiku anu mukulira chifukwa cha machimo anu. Ngati mukufuna kumasuka ku machimo anu, muyenera kukhulupilira m’choonadi cholembedwa, uthenga wabwino wa madzi, mwazi ndi Mzimu.
 
 

KUPEZA CHINSINSI CHA CHIOMBOLO KUDZERA MU UBATIZO WA YESU 

 
Kodi n’chiani chitipangitsa ife kubadwa mwatsopano? 
Ubatizo wa Yesu, imfa Yake pa Mtanda ndi kuukanso Kwake.
 
Baibulo likutiuza kuti aliyense angakhale obadwa mwatsopano kudzera m’mawu a Mulungu, amene sasintha. Tsopano, tiyeni tione pa mawu a mtumwi Petro mu 1 Petro 3:21. “Cimenenso cifaniziro cace cikupulumutsani tsopano, ndico ubatizo.” 
Mu Baibulo, munalembedwa kuti ubatizo wa Yesu ndi chifaniziro chimene chikupulumutsa ife. Onse amene akhulupilira mwa Yesu ayenera kudziwa, osati za ubatizo wathu, koma ubatizo wa Yesu. Ubatizo wa Yesu umapatsa ife ochimwa moyo watsopano. Ukhulupilireni, ndipo muzakhala obadwa mwatsopano ndi kupindula dalitso la chipulumutso. 
Mwa kuzindikira kuti chipulumutso chimapezedwa kudzera m’kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu, tingapulumutsidwe, kukhala olungama ndi kupeza moyo osatha. M’mawu ena, pamene tikhulupilira m’choonadi cha chipulumutso kudzera m’mawu a Mulungu, machimo athu adzayeretsedwa ku nthawi zonse. 
Kubadwa mwatsopano ndi kubadwanso kachiwiri. Ambiri a ife timakonda kuyamba mwa kukhulupilira mwa Yesu ngati chipembezo, ndipo ndiyeno timakhala obadwa mwatsopano kudzera m’chikhulupiliro pamene tazindikira choonadi. Dzina lakuti Yesu likutanthauza, “Pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ace ku macimo ao” (Mateyu 1:21).
Pamene tikukhulupilira mwa Yesu ndi kudziwa bwino zimene Iye anachita kwa mtundu onse wa anthu, ndife omasuka ku machimo athu ndipo ndife obadwa mwatsopano ngati anthu atsopano. Poyamba tinakhulupilira mwa Yesu ngati chipembezo, kenako, pamene tinamvera ndi kukhulupilira uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake, ndife obadwa mwatsopano. 
Kodi choonadi chimene chitipangitsa obadwa mwatsopano n’chiani? Choyamba, ndi ubatizo wa Yesu, kenako mwazi umene anakhetsa pa Mtanda, ndipo chomaliza ndi kuukitsidwa Kwake kwa akufa. Kubadwa mwatsopano kukutanthauza kukhulupilira mwa Yesu ngati Mulungu wathu, Mpulumutsi wathu. Tiyeni tione m’mene anthu a M’chipangano Chakale ankabadwira mwatsopano. 
 
 

MALIPIRO A UCHIMO M’CHIPANGANO CHAKALE: KUIKA MANJA NDI KUPEREKA MWAZI 

 
Kodi uthenga wabwino wa kubadwa mwatsopano ndi chiani m’Chipangano Chakale? Choyamba, tiyeni tiwerenge Levitiko 1 ndi zimene ikunena za kubadwa mwatsopano. 
Mu Levitiko 1:1-5, “Ndipo Yehova anaitana Mose, nanena naye ali m’cihema cokomanako Iye, nati, lankhula ndi ana a Israyeli, nunene nao, ali yense mwa inu akabwera naco copereka ca kwa Yehova, muzibwera naco copereka canu cikhala ca zoweta, ca ng’ombe, kapena ca nkhosa, kapena ca mbuzi. Copereka cace cikakhala nsembe yopsereza ya ng’ombe, azibwera nayo yaimuna yopanda cirema; abwere nayo ku khomo la cihema cokomanako, kuti alandirike pamaso pa Yehova. Ndipo aike dzanja lace pamutu pa nsembe yopsereza; ndipo idzalandiridwa m’malo mwace, imtetezere. Pamenepo aiphe ng’ombeyo pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, abwere nao mwazi, nawaze mwaziwo pozungulira pa guwa la nsembe, lokhala pa khoma la cihema cokomanako.”
Mulungu auza ife mu Levitiko m’mene Israyeli anayenera kugwirizana ndi Mulungu kudzera mu ndondomeko yoperekera nsembe. Ndi choonadi kuti tonse tiyenera kudziwa ndi kumvetsetsa. Motero tiyeni tionenso mawu amenewa. 
Mulungu anaitana Mose ndi kulankhula naye pa chihema chokomanako. Kunali kutetezera machimo a Israyeli. Pamene anthu a ku Israyeli anali kuchita machimo a kusamvera lamulo la Mulungu, ankadzitetezera machimo awo mwa kupereka chiweto chopanda chilema kwa Mulungu. 
Nyama zoperekedwa nsembe zimenezi ziyenera kukhala zija zosankhidwa ndi Mulungu ndipo ziyenera kukhala zopanda chilema. Ndiponso, zinkayenera kuperekedwa molingana ndi mwambo oikidwa ndi Mulungu. Ndondomeko yoperekera nsembe inali yotere. 
Ngati aliyense wachimwa m’nthawi ya Chipangano Chakale, ankayenera kupereka nsembe pamaso pa Mulungu kuti akhululukidwe uchimo. Choyomba, nsembe inayenera kukhala yopanda chilema, ndipo ochimwa anayenera kuika manja pamutu pa nsembeyo kuti apereke machimo ake pa mutu pake. 
Pambuyo pakuti yaphedwa, mwazi wake unkayenera kuikidwa pa nyanga za guwa lansembe, ndipo mwazi otsalira onse unali kuthiridwa pansi pa guwa. Uwu unali mwambo wa chihema choyera umene Mulungu anapereka kwa anthu Ake ngati dalitso la chiombolo. 
Lamulo ndi malamulo a Mulungu ali ndi ndi ndime zokwanira 613 onena zimene “ayenera kuchita,” kapena “sayenera kuchita.” Mulungu anapereka lamulo ndi malamulo Ake kwa anthu a ku Israyeli. Ngakhale kuti anthu ankadziwa kuti lamulo ndi malamulo a Mulungu anali abwino, sanathe kukhala mwa iwo chifukwa aliyense anabadwa ndi mitundu khumi ndi iwiri ya machimo imene anatenga kwa Adamu. 
Motero, anataya mwayi ochita zabwino pamaso pa Mulungu. Israyeli anataya mwayi okhala olungama. M’malomwake, sanadzithandize koma kupitiliza kumachita machimo, ngakhale pamene ankayesa kwambiri kukhala omasuka ku uchimo. Ndi kwatsoka kwa mtundu wa munthu kubadwa ndi kufa ngati ochimwa. 
Koma Mulungu, m’chifundo Chake chachikulu, anapatsa anthu Ake ndondomeko yoperekera nsembe imene ankayenera kutetezera machimo awo. Iye anapereka mwambo wa chihema choyera kotero kuti anthu a ku Israyeli ndi anthu onse a dziko aomboledwe ku machimo awo. Iye anabvumbulutsa kudzera mu ndondomeko yoperekera nsembe chikondi Chake choyera cha mtundu wa munthu. Iye anaonetsa dziko njira yachipulumutso. 
Mulungu anapatsa anthu ndondomeko yoperekera nsembe ndi kusankha nyumba ya Levi kuti itsogolere nsembe. Mwa mafuko khumi ndi awiri a Israyeli, nyumba yokha ya Levi ndi imene inasankhidwa kuti itumikire nsembe ya anthu a Israyeli. 
Mose ndi Aroni anali a nyumba ya Levi. Ndipo Baibulo inalemba malamulo ndi zoyenera zolamulira nsembe ya chihema choyera, uthenga wabwino wa chitetezero cha machimo mwa kuika manja. 
Motero, pamene tikuzindikira poyera mwambo waunsembe wa Alevi, tingakhale obadwa mwatsopano ife tokha. Ndi chifukwa chake tiyenera kuwerenga mawu a Mulungu chifukwa cha nsembe ya chihema choyera. Iyi ndi mbali yofunika kwambiri ya M’chipangano Chakale. Pomaliza, ngati tabwera ku Chipangano Chatsopano, tili ndi madalitso akubadwa mwatsopano kudzera mwa madzi ndi Mzimu. 
 

CHITETEZERO CHA MACHIMO MU CHIPANGANO CHAKALE 
 
Kodi makhalidwe a Mulungu ndi chiani?
Chilungamo ndi Chikondi 
 
Mulungu anaitana Mose, wa nyumba ya Levi, ku chihema choyera chosonkhanira ndi kudzodza m’bale wake Aroni kukhala wansembe wamkulu. Aroni anali kupereka machimo a anthu pa nsembe yauchimo.
Ichi ndi chimene Mulungu ananena kwa Mose monga analembera mu Levitiko 1:2. “Lankhula ndi ana a Israyeli, nunene nao, ali yense mwa inu akabwera naco copereka ca kwa Yehova, muzibwera naco copereka canu cikhala ca zoweta, ca ng’ombe, kapena ca nkhosa, kapena ca mbuzi.” Mulungu ananena apa nsembe zoyenera kuperekedwa. Ngati aliyense wa anthuwo akufuna chitetezero cha machimo ake, ankayenera kupereka ng’ombe yamphongo kapena nkhosa yochokera m’ziweto zake. 
Mulungu anawauzanso, “Copereka cace cikakhala nsembe yopsereza ya ng’ombe, azibwera nayo yaimuna yopanda cirema; abwere nayo ku khomo la cihema cokomanako, kuti alandirike pamaso pa Yehova.” (Levitiko 1:3).
Nsembe inali kuvomerezedwa ndi Mulungu m’malo mwa moyo wa munthu amene anayenera kufa chifukwa cha machimo ake. Israyeli ankapereka machimo awo mwa kuika manja awo pamitu pa nyamazo. Nyama yoperekedwa nsembe inayenera kuperekedwa ndi munthu mwa kufuna kwake. Tsopano, tiyeni tione chimene ndime yachinayi ikunena. 
“Ndipo aike dzanja lace pamutu pa nsembe yopsereza; ndipo idzalandiridwa m’malo mwace, imtetezere.” Nsembeyo inali kuvomerezedwa ndi Mulungu. Pamene wochimwa anali kuika manja ake pamutu pa nsembe yopsereza, machimo ake anali kuperekedwa pa mutu nyama. Motero ochimwa anayenera kuika manja ake pamutu pa nsembeyo pamaso pa Mulungu, kotero kuti Mulungu aivomereze ndi kupereka chitetezero cha machimo ake. 
Munthu ankapereka nsembe kenako ankapha nyamayo ndi kuika mwazi wake pa nyanga za pa guwa ndi kuthira mwazi otsala pansi pa guwa. Kuti alipire machimo ake ndi kukhala omasuka kwa iwo, munthu ankafunika kupereka nsembe mogwirizana ndi malamulo loikidwa ndi Mulungu. 
Munalembedwa mu Levitiko 1:5, “Pamenepo aiphe ng’ombeyo pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, abwere nao mwazi, nawaze mwaziwo pozungulira pa guwa la nsembe, lokhala pa khoma la cihema cokomanako.” Mkati mwa chihema, cha pa khomo, panali guwa la nsembe yopsereza ndi nyanga pa ngondya zinayi. 
Akaika manja ake pa mutu pa nsembe yopsereza kuti apereke machimo ake, ochimwa anayenera kupha nyama yoperekedwa nsembe, ndipo wansembe ankawaza mwazi wake pa nyanga. Nyanga za pa guwa zikuimira chiweruzo cha machimo. Motero, kuika mwazi pa nyanga zimenezi kukutanthauza kuti nyama yakhetsa mwazi kuti ilipire machimo m’malo mwa ochimwa. Pamene Mulungu wayang’ana mwazi pa nyanga za pa guwa, anali kuononga machimo a ochimwa. 
N’chifukwa chiyani nsembe yauchimo inkayenera kukhetsa mwazi? Chifukwa “mphoto yace ya uchimo ndi imfa” (Aroma 6:23) ndipo chifukwa chakuti moyo wa thupi uli m’mwazi. Motero kunalembedwa mu Aheberi, “Wopanda kukhetsa mwazi kulibe kumasuka” (Ahebri 9:22). Motero, kukhetsa mwazi kwa nsembe yauchimo kunakwaniritsa lamulo la Mulungu, limene likunena kuti mphoto yauchimo ndi imfa. 
Mwa ufulu onse, mwazi operekedwa akanakhala ochokera kwa ochimwa, koma nsembe yauchimo inakhetsa mwazi m’malo mwake chifukwa cha chitetezero cha machimo. Wansembe ndiyeno ankaika mwazi pa nyanga za pa guwa kuonetsa kuti mphoto ya uchimo inalipiridwa. 
Ngati tingawerenge Chivumbulutso 20:11-15 mu Chipangano Chatsopano, Tingaone kuti nyanga zikusonyeza Bulu la Chiweruzo. Motero kuika mwazi pa nyanga ndi kuika mwazi pa Buku la chiweruzo. Kunali kuonetsa kuti chiweruzo cha machimo chinakwaniritsidwa mwa kuika manja ndi mwazi wa nsembe yauchimo. 
 

MACHIMO ANALEMBEDWA M’MALO AWIRI 
 
Machimo onse a mtundu wa anthu pamaso pa Mulungu analembedwa m’malo awiri. Imodzi ndi pansi pa mitima yawo, ndipo ina ndi Buku la Chiweruzo lotsegulidwa pamaso pa Mulungu. 
Kunalembedwa mu Yeremiya 17:1, “Cimo la Yuda lalembedwa ndi peni lacitsulo, ndi nsoga ya diamondi; lalembedwa pa colembapo ca m’mtima mwao, ndi pa nyanga za maguwa ansembe anu.” 
Mu Levitiko 17:11, akunena kuti, “Pakuti moyo wa nyama ukhala m’mwazi.” Mwazi ndi moyo wathupi, ndipo machimo athu angalipiridwe kokha ndi mwazi umenewu. Motero, mwazi unkaikidwa pa nyanga za pa guwa. Monga mwa lamulo, pafupifupi zinthu zonse zinayeretsedwa ndi mwazi, ndipo wopanda kukhetsa mwazi kulibe kumasuka (Ahebri 9:22).
“Ndipo asende nsembe yopsereza, ndi kuikadzula ziwalo zace. Ndipo ana a Aroni asonkhe moto pa guwa la nsembe, ndi kukonza nkhuni pa motopo; ndi ana a Aroni, ansembewo akonze ziwalozo, mutu ndi mafuta pa nkhuni ziri pa moto wa pa guwa la nsembe; koma atsuke ndi madzi matumbo ace ndi miyendo yace ndi wansembe atenthe zonsezi pa guwa la nsembe, zikhale nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya pfungo lokoma la kwa Yehova” (Levitiko 1:6-9).
Ndiyeno wansembe ankadula nsembe yopsereza m’ziwalo ndi kuika ziwalozo pamoto wa pa guwa. Mwambo umenewu unali kutanthauza kuti pamene anthu achimwa pamaso pa Mulungu, anayenera kufa m’njira imeneyo ndi kukhetsa mwazi ndi kuponyedwa mu moto wa gehena. Komabe, chiweruzo chinachitika kudzera mu nsembe yauchimo, kotero kuti anthu athe kutetezera machimo awo. 
Nsembe zopsereza inali mwambo wa chiweruzo cha lamulo lachilungamo la Mulungu. Mulungu anagwirizanitsa malamulo Ake onse, lamulo la chilungamo ndi lamulo la chikondi, mu mwambo wa chitetezero cha machimo a mtundu wa anthu. 
Chifukwa Yesu ndi chilungamo, anayenera kuweruza ndi kuwalamula kuti aphedwe. Koma, chifukwa chakuti Iyenso amakonda anthu Ake, anawalola kuti apereke machimo awo pa nsembe yauchimo. Mu Chipangano Chatsopano, chifukwa Ambuye wathu ankatikonda ife, anabatizidwa ndi kupachikidwa kukhala nsembe yauchimo ya ife ochimwa. Ubatizo wa Yesu ndi imfa Yake ya pa Mtanda inachotsa machimo onse a dziko. 
 

CHITETEZERO CHA MACHIMO A TSIKU LIMODZI M’CHIPANGANO CHAKALE 
 
Kodi nsembe yauchimo yopanda chilema inkaimira ndani mu Chipangano Chakale?
Yesu Kristu Jesus
 
Tiyeni tiwerenge kuyambira pa Levitiko 4:27. “Ndipo akacimwa wina wa anthu a m’dziko, osati dala, pa cina ca zinthu ziri zonse aziletsa Yehova, naparamula; akamdziwitsa kucimwa kwace adacimwako, azidza naco copereka cace mbuzi yaikazi, yopanda cirema, cifukwa ca kucimwa kwace adakucita. Aike dzanja lace pamutu pa nsembe yaucimo, naiphe nsembe yaucimo pamalo pa nsembe yopsereza. Ndipo wansembe atengeko mwazi ndi cala cace, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wonse patsinde pa guwa la nsembe. Nacotse mafuta ace onse, monga umo amacotsera mafuta pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo awatenthe pa guwa la nsembe akhale pfungo lokoma la kwa Yehova; ndi wansembe amcitire comtetezera, ndipo adzakhululukidwa” (Levitiko 4:27-31).
Mbadwo wa Adamu, anthu a mu Israyeli, ndi anthu onse a kudziko anabadwa m’dzikoli lodzala ndi uchimo. Motero mitima yathu ndi yodzala ndi uchimo. Muli mitundu yonse yauchimo mkati mwa mtima wa munthu: maganizo oipa, ziwerewere, zigololo, kupha, kuba, masiriro ndi kupusa. 
Pamene ochimwa akufuna kudzitetezera ku machimo a tsiku limodzi, ankayenera kubweretsa nyama yopanda chilema ku chihema choyera. Kenako ankafunika kuika manja ake pa mutu pa nyama kuti apereke machimo ake, kupha nsembe ndi kupereka mwazi ake kwa wansembe kuti apereke pamaso pa Mulungu. Wansembe kenako ankachita mwambo onse waunsembe kotero kuti ochimwa akhululukidwe ku machimo ake. 
Kopanda lamulo ndi malamulo a Mulungu, anthu sakanadziwa kuti achimwa kapena ai. Pamene taziona tokha kudzera mu chilamulo ndi malamulo a Mulungu, timazindikira machimo athu. Machimo athu sakuweruzidwa mwa kuchita bwino kwathu, koma mwa lamulo ndi malamulo a Mulungu. 
Anthu wamba a mu Israyeli anali ankachimwa, osati chifukwa chakuti anali kufuna, koma chifukwa chakuti anabadwa ndi mitundu yonse yauchimo m’mitima yawo. Machimo amene munthu akuchita chifukwa cha kufoka kwake akutchedwa kuti zolakwika. Uchimo ukuphatikizapo zolakwika zonse ndi zoipa za mtundu wa anthu. 
Anthu onse ndi operewera. Monga anthu onse a mtundu wa Israyeli naonso anali operewera, anali ochimwa ndipo anali kuchita machimo. Zolakwa zathu zonse ndi mphulupulu zathu zingagawidwe m’njira yotere. Pamene tili ndi maganizo oipa m’maganizo mwathu, amatchedwa machimo, ndipo pamene tawachita, amatchedwa zolakwa. Machimo a kudziko akuphatikizapo mitundu yonse. 
M’chipangano Chakale, machimo anali kuperekedwa pamutu pa nsembe yauchimo mwa kuika manja. Patsogolo pake, ochimwa anali kukhala opanda chimo ndipo motero sankayenera kufa chifukwa cha machimo ake. Ndondomeko yoperekera nsembe ndi chithunzi cha chiweruzo cha chilungamo ndiponso chikondi cha Mulungu. 
Chifukwa Mulungu analenga ife kuchokera ku fumbi, tinali dothi wamba pachiyambi. Kuika mwazi pa nyanga za pa guwa ndi kuthira otsala pansi pa guwa kukutanthauza kuti Israyeli analipira malipiro a machimo awo ndipo anafufuta machimo onse kuchokera pansi pa mitima yawo. 
Wansembe adzatentha mafuta pa guwa kuti chikhale chonunkhira kwa Ambuye. Mafuta M’baibulo akutanthauza Mzimu Oyera. Motero, kuti atetezere machimo athu, tiyenera kuchita m’njira imene Mulungu analamulira. Ndipo tiyeneranso kuchitenga m’mitima yathu chitetezero cha machimo athu m’njira imene Mulungu akuombola moyenera. 
Mulungu anauza anthu a ku Israyeli kuti nsembe yauchimo iyenera kukhala mwana wa nkhosa, mbuzi kapena mwana wa ng’ombe. Nsembe yauchimo ya m’Chipangano Chakale inali yosankhika. Mwana wan g’ombe ndi nyama yopanda chilema. Chifukwa chimene nsembe yauchimo inafunikira kukhala yopanda chilema chinali chakuti zinali kubvumbulutsa Yesu Kristu amene anabadwa mwa Mzimu Oyera nkukhala nsembe yauchimo ya mtundu wa anthu onse. 
Anthu a m’Chipangano Chakale anali kupereka machimo awo mwa kuika manja awo pa mutu pa nsembe yauchimo yopanda chilema. Wansembe ankapereka nsembe kuti alipire machimo awo. Umu ndi m’mene anthu a mu Israyeli anali kutetezera machimo ao. 
 
 

MWAMBO WA PA TSIKU LA CHITETEZERO CHA MACHIMO

 
Kodi n’chifukwa chiani anthu a ku Israyeli anayenera kupereka nsembe pa Tsiku Lachitetezero cha machimo? 
Chifukwa anapitiliza kuchimwa kufikira imfa. Kupereka nsembe ya uchimo masiku onse sikunawayeretse pamaso pa Mulungu.
 
Komabe, popeza ankayenera kupereka nsembe nthawi zonse pamene achita tchimo, kunali kosatheka kupereka nsembe zonse zimene anali kufuna kuti atetezere machimo awo. Choncho, pang’ono pang’ono, anakhala otaika. Kunalu kuoneka ngati ndi ntchito yosatha kutetezera machimo awo masiku onse ndipo anayamba kumva ngati angasiye mwambo umenewu pamodzi. 
Zilibe kanthu kuti tikuyesa motani, sitingapereke nsembe zokwanira za machimo athu onse. Motero malipiro oona a machimo athu ayenera kupatsidwa kudzera mu chikhulupiliro cha mtima wathu mu lamulo la chipulumutso limene Mulungu anakonzera ife. 
Chifukwa cha kufoka kwathu, mulimonse m’mene tingayesere kukhala mwa lamulo la Mulungu, timakhala chabe odzindikira m’mene tilili kuperewera komanso kufoka kwathu. Motero Mulungu anapatsa anthu a ku Israyeli njira yakuti atetezere machimo onse a pa chaka onse kamodzi (Levitiko 16:17-22).
Kunalembedwa mu Levitiko, “Ndipo lidzakhala kwa inu lemba losatha; mwezi wacisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi la mweziwo, mudzicepetsa, osagwira nchito konse, kapena wa m’dziko, kapena mlendo wakukhala pakati panu; popeza tsikuli adzacitira inu cotetezera, kukuyeretsani; adzakuyeretsani, kukucotserani zoipa zanu zones pamaso pa Yehova. Likhale kwa inu sabata lakupumula, kuti mudzicepetse; ndilo lemba losatha” (Levitiko 16:29-31).
Motero, anthu a ku Israyeli anali ndi mtendere wa m’maganizo kamodzi pa chaka pamene wansembe wamkulu ankatumikira nsembe ya chitetezero pa tsiku lakhumi la mwezi wa chisanu ndi chiwiri ya machimo onse amene anthu anachita chaka chonse. Pamene machimo awo anatsukidwa, chikumbu mtima chawo chinali pa mtendere pa tsiku limenelo. 
Pa tsiku la khumi la mwezi wa chisanu ndi chiwiri, wamkulu wansembe Aroni, ngati woimilira wa Israyeli, anayenera kutumikira nsembe yachitetezero cha machimo. Pa nthawi imeneyi, ansembe ena sankalowa mu chihema choyera. Choyamba pa zonse, Aroni anayenera kutumikira nsembe yotetezera machimo ake ndi nyumba yake asanachitire anthu onse a Israyeli chifukwa iye ndi a m’nyumba yake nawonso anali atachimwa. 
Iye ankatumikira nsembe ya anthu motere. “Ndipo atenge mbuzi ziwirizo naziimike pamaso pa Yehova pa khomo pa cihema cokomanako. Ndipo Aroni ayese maere pa mbuzi ziwirizo; maere amodzi kwa Yehova, ndi amodzi kwa Azazeli. Ndipo Aroni abwere nayo mbuzi imene adaigwera maere a Yehova, naiyese nsembe yaucimo. Koma mbuzi imene adaigwera maere a Azazeli, aiike yamoyo pamaso pa Yehova, kuti acite nayo cotetezera, kuitumiza kucipululu ikhale ya Azazeli.” (Levitiko 16:7-10). 
Atatha kuchita mwambo wa chitetezero cha machimo a nyumba yake ndi iyeyekha, Aroni, “ankachita maere a mbuzi ziwiri.” Maere amodzi anali a Ambuye ndipo ena anali a ya mbuzi yamoyo,“Azazeli.” 
Choyamba, imodzi mwa mbuzi ziwiri inaperekedwa kwa Ambuye. Pano, wamkulu wansembe ankaika manja ake pa mbuzi m’malo mwa anthu kuti apereke machimo amene anachita mkati mwa chaka. 
Mwazi ankaperekedwa ku mpando wachitetezero mkati mwa Malo Oyeretsetsa ndi kuuwaza kasanu ndi kawiri. Anthu a ku Israyeli anali kukhululukidwa machimo awo onse a chaka chimene chatha, M’malo mwa anthu a ku Israeli kufa chifukwa cha machimo awo, wamkulu wansembe Aroni ankapereke machimo pa mutu pa nsembe yauchimo ndi kuisiya kuti inyamule chiweruzo chawo. Ndiyeno ankaperekanso nsembe mbuzi ina yamoyo pamaso pa Mulungu. Iyo inali nsembe imene inali kuperekedwa kwa anthu. 
 

CHIFUKWA CHA ANTHU
 
Pamaso pa anthu onse, Aroni ankaika manja ake pa mbuzi yachiwiri ndi kuulula pamaso pa Mulungu. “Ambuye, anthu a ku Israeli anachita zakupha, chigololo, kuba, kusilira, chinyengo…ndipo anali kugwadira mafano. Iwo sanasunge Sabata kukhala loyera, iwo anaitana pa dzina Lanu mwachaba, ndipo anaphwanya ndime zonse za Chilamulo ndi malamulo Anu.” Kenako ankachotsa manja ake. Ndi chimenechi, machimo onse a anthu a chaka chonse anali kuperekedwa ku nsembe yauchimo.
Tiyeni tiwerenge Levitiko 16:21. “ndipo Aroni aike manja ace onse awiri pamutu pa mbuzi yamoyo, ndi kubvomereza pa iyo mphulupulu zonse za ana a Israyeli, ndi zolakwa zao zonse, monga mwa zocimwa zao zonse; naike izi pamutu pa mbuziyo, ndi kuitumiza kucipululu ndi dzanja la munthu wompangiratu.” Mbuzi ya azizeli ndiyeno inali kuzungulira m’chipululu ndi kufa pamodzi ndi machimo a anthu a ku Israyeli pa mutu wake. Mbuzi yamoyo, “Azazeli” mu Chihebri, kutanthauza “kuchotsa”. Zikutanthauza kuti inali kuchotsedwa pamaso pa Ambuye, m’malo mwa anthu onse a Israyeli. 
Motero, machimo a Israyeli anali kuperekedwa pa mbuzi yamoyo kudzera mwa kuika manja a Aroni. Mwa njira imeneyi Israyeli anali kukhululukidwa machimo awo. Pamene ankaona wamkulu wansembe kuti waika manja pa mbuzi ndi kuiona ikutsogoleredwa ku chipululu, anthu onse a Israyeli amene anakhulupilira mu mwambo wa chitetezero cha machimo anali ndi chidaliro cha chitetezero cha machimo awo. Mwambo onse wa M’chipangano Chakale unali chithunzi cha ‘uthenga wabwino wa kubadwa mwatsopano’ wa m’Chipangano Chatsopano. 
Mu Chipangano Chakale, kuika manja ndi mwazi wa nsembe unali uthenga wabwino wa chipulumutso cha uchimo. Chinakhalabe choyenera chimodzimodzi ndi mu Chipangano Chatsopano. 
 

UTHENGA WABWINO WA CHIOMBOLO MU CHIPANGANO CHATSOPANO 
 
Mu Chipangano Chatsopano, kodi machimo onse a anthu anaonongedwa motani? 
Kunalembedwa mu Mateyu 1:21-25, “Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamucha dzina lace Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ace ku macimo ao. Ndipo zonsezi zinakhala kuti cikacitidwe conenedwa ndi Ambuye mwa mneneri, ndi kuti, onani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, ndipo azamucha dzina lace Emanueli; ndilo losandulika, Mulungu nafe. Ndipo Yosefe anauka tulo tace, nacita monga anamuuza mngelo wa Ambuye, nadzitengera yekha mkazi wace; ndipo sanamdziwa iye kufikira atabala mwana wace; namucha dzina lace Yesu.”
Ambuye wathu Yesu anabwera kudzikoli m’dzina la Emanueli kuti apulutse mtundu onse ku uchimo. Motero anatchedwa kuti Yesu. Yesu anabwera kuzachotsa machimo onse a dziko. Iye anabwera m’thupi la umunthu kuti akhale Mpulumutsi wa mtundu wa anthu. Iye anakwaniritsa chipulumutso chathu ndi kutimasula ku uchimo kwamuyaya. 
 
 

UTHENGA WABWINO WAKUBADWA MWATSOPANO 

 
Ndipo kodi Yesu anatimasula motani ku machimo athu? Iye anatero kudzera mu ubatizo Wake. Tiyeni tione pa Mateyu 3:13-17. 
“Pamenepo Yesu anacokera ku Galileya nadza ku Yordano kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye. Koma Yohane anati amkanize, nanena, Ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi? Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero. Pamenepo anamlola Iye. Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anaturuka m’madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye; ndipo onani, mau akucokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera” (Matthew 3:13-17). 
Mu Chipangano Chatsopano, Pamene Yesu anakhala ndi zaka makumi atatu, anadza kwa Yohane Mbatizi pa Yordano. Iye anabatizidwa ndi iye ndi kunyamula machimo onse a ochimwa. Mwa kuchita choncho, anakwaniritsa chilungamo chonse cha Mulungu.
 
 

KODI N’CHIFUKWA CHIANI YESU ANABATIZIDWA PA YORDANO? 

 
Kodi n’chiani chinabvumbulitsidwa mu uthenga wabwino? 
Chilungamo cha Mulungu 
 
Tiyeni tsopano tione pa chochitika pamene Wamkulu Wansembe wakumwamba anakuna ndi wamkulu wansembe wa mtundu wa anthu. Apa tingaone chilungamo cha Mulungu kudzera mu ubtizo umene unatetezera chitetezero cha machimo onse a dziko. 
Yohane Mbatizi, iye amene anabatiza Yesu, anali wamkulu mwa iwo amene anabadwa kwa akazi. Yesu anachitira umboni mu Mateyu 11:11, “Sanauke wakubadwa mwa akazi munthu wamkuru woposa Yohane Mbatizi.” Monga machimo a anthu ankaonongedwera pamene wamkulu wansembe Aroni ankaika manja pamutu pa nsembe yauchimo pa Tsiku la chitetezero cha machimo, mu Chipangano Chatsopano, machimo onse a dziko anaonongedwa pamene Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. 
Uthenga abwino wa kubadwa mwatsopano ndi uthenga wabwino wa chitetezero chanthunthu cha machimo athu onse, akale, atsopano ndi akutsogolo. Motero uthenga wabwino wachiombolo kudzera mu ubatizo wa Yesu unali uthenga wabwino umene Mulungu anaika kuti akwaniritse chilungamo Chake, chimene chinapulumutsa anthu onse a dziko. Yesu anabatizidwa m’njira yabwino kwambiri kuti atetezere machimo a dziko. 
Kodi Kukwaniritsa “chilungamo chonse” kukutanthauzanji? Kukutanthauza kuti Mulungu anatsuka machimo onse a kudziko m’njira yoyenera kwambiri. Yesu anabatizidwa kuti atsuke machimo onse a mtundu wa anthu. “Pakuti m’menemo caonetsedwa cilungamo ca Mulungu cakucokera kucikhulupiriro kuloza kucikhulupiriro” (Aroma 1:17). 
Chilungamo cha Mulungu chinaonetsedwa mu chisankho chake kuti atumize Mwana Wake Yesu kudzikoli kuti atsuke machimo onse a dziko kudzera mu ubatizo Wake ndi Yohane Mbatizi ndiponso imfa Yake ya pa Mtanda. 
Mu Chipangano Chatsopano, chilungamo cha Mulungu chinaonekera kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Tinakhala olungama chifukwa Yesu ananyamula machimo onse a mtundu wa anthu pafupifupi zikwi ziwiri zapitazo pa Yordano. Pamene tinavomereza chipulumutso cha Mulungu m’mitima yathu, chilungamo cha Mulungu chinakwaniritsidwa mwa zoona. 
“Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero. Pamenepo anamlola Iye. Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anaturuka m’madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye; ndipo onani, mau akucokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera” (Mateyu 3:15-17). 
Ndimeyi ikubvumbulutsa kuti Mulungu Iyeyekha anachitira umboni kuti ubatizo wa Mwana Wake unakwaniritsa chilungamo chonse cha chipulumutso. Iye anali kutiuza kuti, “Yesu, amene anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi, tsopano ndi Mwana Wangadi.” Mulungu anachitira umboni kuti Mwana Wake anabatizidwa kuti atetezere machimo a mtundu wa anthu. Iye anachita zimenezo, kotero kuti ntchito yoyera ya Mwana Wake, Yesu, isakhale yachabe. 
Yesu ndi Mwana wa Mulungu ndiponso Mpulumutsi wa ochimwa a kudziko. “mwa Iyeyu ndikondwera,” anatero Mulungu. Ndi zoonadi kuti Yesu anamvera chifuniro cha Atate ndi kunyamula machimo onse a mtundu wa anthu kudzera mu ubatizo Wake. 
Mawu akuti ubatizo akutanthauza “kutsukidwa, kupereka kwa, kukwiriridwa.” Chifukwa machimo athu onse anaperekedwa pa Yesu pamene anabatizidwa, chimene tiyenera kuchita ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino kuti tipulumutsidwe ku machimo a dziko. 
Kukwaniritsidwa kwa uneneri onse wa chipulumutso mu Chipangano Chakale unamalizika kudzera mu ubatizo wa Yesu mu Chipangano Chatsopano. Motero uneneri mu Chipangano Chakale unapeza oyanjana nawo mu Chipangano Chatsopano. Monga anthu a ku Israyeli anatetezera machimo awo kamodzi pa chaka mu Chipangano Chakale, machimo a anthu anaperekedwa kwa Yesu ndi kuonongedwa kwamuyaya mu Chipangano Chatsopano. 
Levitiko 16:29 ndi chifaniziro cha Mateyu 3:15. Yesu anabatizidwa kuti achotse machimo onse a dziko. Tithokoza ku ubatizo Wake, onse amene akukhulupilira mu chikhululukiro Chake chosatha anapulumutsidwa; machimo awo onse anafufutidwa kuchokera pansi pa mitima yawo. 
Ngati simukuzindikira ndi kukhulupilira mu mtima wanu choonadi cha ubatizo wa Yesu ndi imfa Yake ya pa Mtanda, simungayeretsedwe ku machimo anu zilibe kanthu kuti mukukhala ndi moyo otani. Kudzera mu ubatizo wa Yesu yekha ndi pamene mawu a Mulungu anakwaniritsidwa ndipo machimo athu amafufutidwa. Chipulumutso choona chipezedwa kudzera mu chiombolo cha machimo athu onse, m’mawu ena, kudzera mu ubatizo wa Yesu. 
Ndi chimenechi m’maganizo, kodi muzachita chiani? Kodi mudzavomera chipulumutsochi mu mtima mwanu? Kapena simudzatero? Awa simawu a munthu, koma a Mulungu Iyeyekha. Yesu anafa pa Mtanda chifukwa anachotsa machimo athu onse kudzera mu ubatizo Wake. Kodi simukugwirizana nazo kuti kupachikidwa kwa Yesu kunali chifukwa cha ubatizo Wake? 
Kunalembedwa mu Aroma 8:3-4, “Pakuti cymene cilamulo sicinathe kucita, popeza cinafoka mwa thupi, Mulungu anatuniza Mwana wace wa Iye yekha m’cifanizo ca thupi la ucimo, ndi cifukwa ca ucimo, natsutsa ucimo m’thupi; kuti coikika cace ca cilamulo cikakwaniridwe mwa ife, amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu.” 
Chifukwa ife monga anthu ofoka sitingathe kusunga lamulo ndi malamulo a Mulungu chifukwa kufoka kwa thupi, Yesu anachotsa machimo onse a thupi mwa kuwanyamula pa Iyeyekha. Ichi ndi choonadi cha ubatizo wa Yesu. Ubatizo wa Yesu unatanthauziratu imfa Yake ya pa Mtanda. Iyi ndi nzeru ya uthenga wabwino oyamba wa Mulungu. 
Ngati munali kungokhulupilira mu imfa ya Yesu ya pa Mtanda, bwererani tsopano ndipo vomerani mu mtima mwanu uthenga wabwino wa chipulumutso kudzera mu ubatizo wa Yesu. Kenako, ndipo kutero kokha, ndi pamene mungakhale mwana oona wa Mulungu. 
 

UTHENGA WABWINO OYAMBA
 
Kodi uthenga wabwino oyamba n’chiani?
Uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu 
 
Uthenga wabwino oyamba ndi uthenga wa chitetezero cha machimo. Uwu ndi uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu, imfa Yake ndi kuukanso umene Mulungu anavumbulutsa kwa ife. Yesu Kristu anatsuka uchimo onse pa nthawi imodzi mwa kubatizidwa pa Yordano ndipo kudzera mwa ichi anapatsa chipulumutso kwa iwo onse amene akhulupilira mu choonadi chimenechi. Chifukwa cha chikhulupiliro chathu, machimo athu onse akutsogolo nawonso anatsukidwa. 
Tsopano, aliyense amene akhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake a pa Mtanda anapulumutsidwa ku machimo onse a kudziko kwamuyaya. Kodi mukukhulupilira? Ngati yankho lanu ndi yakuti “Inde, ndimatero.” Ndiyeno muzakhala olungama mwa choona. 
Tiyeni mwachidule timalize zochitika zimene zinachitika Yesu atabatizidwa. Mu Yohane 1:29, kunalembedwa kuti “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” 
Yohane Mbatizi anachitira umboni kuti Yesu anali Mwana wa nkhosa wa Mulungu amene anachotsa uchimo wa dziko. Yohane Mbatizi anapereka kwa Yesu machimo onse a dziko pamene anabatiza Iye pa Yordano. Kuonjezerapo, chifukwa Yohane Mbatizi iyeyekha anabatiza Yesu, anatha kuchitira umboni, “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” Yesu anabatizidwa ndi kuchotsa machimo a dziko, uwu ndi uthenga wabwino wa kubadwa mwatsopano. 
 
 
“Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” (Yohane 1:29). Yesu anachotsa machimo onse a dziko kudzera mu ubatizo Wake. 
Machimo amene munachita kuyambira pakubadwa kufikira zaka zanu khumi anaphatikizidwa ku machimo a dziko. Kodi mukhulupilira kuti machimo amenewo anaperekedwa kwa Yesu? ― Inde, ndikukhulupilira. ― Kodi nanga zolakwa zanu kuyambira zaka 11 kufikira 20? Kodi mukukhulupilira kuti machimo amenewo anaperekedwa kwa Yesu? ― Inde, ndikukhulupilira. ― 
Kodi machimo amene muzachita mtsogolo ali pakati pa machimo a dziko? ― Inde, nawonso anaphatikizidwa. ― Nanga, kodi anaperekedwa kwa Yesu? ― Inde, anaperekedwa. ― Kodi zoonadi mukukhulupilira kuti machimo anu anaperekedwa kwa Yesu? ― Inde, ndikukhulupilira. ― Kodi mumakhulupilira kuti machimo onse a dziko anaperekedwa kwa Yesu kudzera mu ubatizo Wake? ― Inde, ndikukhulupilira. ―
Kodi mukufunadi kupulumutsidwa ku machimo a kudziko? Ngati mukufuna, khulupilirani mu uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake pa Mtanda. Mukangokhulupilira, mwapulumutsidwa. Kodi mumakhulupilira zimenechi? Ichi ndi chipulumutso choonadi cha kubadwa mwatsopano. Ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake ndi uthenga wabwino oyamba wa kubadwa mwatsopano. Ndi dalitso lochokera kwa Mulungu la ochimwa onse a kudziko. 
Kukhulupilira mu chipulumutso cha kubadwa mwatsopano kudzera mu ubatizo wa yesu ndi mwazi wake pa Mtanda, kuyang’ana ku chikondi Chake komanso kukhala ndi chikhulupiliro choona ndi kubadwadi mwatsopano. Zizindikiro za kubadwa mwatsopano ndi madzi komanso mwazi wa Yesu. Muyenera kungovomereza mawu a choonadi olembedwa mu Baibulo. 
 

CHIPEMBEZO NDI CHIKHULUPILIRO 
 
Kodi tili ndi umboni otani m’mitima ya obadwa mwatsopano? 
Kuti Yesu anachotsa machimo athu onse ndi ubatizo Wake ndiponso mwazi
 
Tanthauzo La chipembezo ndi kukhulupilira mwa Yesu mogwirizana ndi maganizo ake a munthu, kukana mawu oyera a Mulungu. Komabe, chipulumutso cha uchimo chili kutali ndi maganizo a munthu. Chikhulupiliro ndi kukhulupilira mawu onse a m’Chipangano Chakale ndi Chatsopano, kukana maganizo a munthu. Ndi kuona m’mene kunalembedwera m’Baibulo ndi kuvomereza chipulumutso kudzera mwa madzi ndi mwazi: ubatizo wa Yesu ndi imfa Yake ya pa Mtanda. Munthu angapulumutsidwe mwa kuika mu mtima mwake nzeru ya uthenga wabwino oyamba. 
Popanda ubatizo wa Yesu kulibe kupereka machimo athu, ndipo popanda kukhetsa mwazi kukanakhala kulibe chikhululukiro cha machimo. Machimo athu onse anaperekedwa kwa Yesu asanawapereke pa Mtanda ndi kukhetsa mwazi m’malo mwa ife. Pamene tikukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake pa Mtanda, mu kubadwa mwatsopano kudzera mu uthanga wabwino, timakhala omasuka ku machimo onse a dziko. 
Chikhulupiliro choona ndi kukhulupilira kuti Yesu Kristu anatiyeretsa ife kwanthunthu ku machimo athu onse pamene anabatizidwa; ndi kukhulupilira kuti Iye ananyamula chiweruzo cha machimo athu pa Mtanda. Tiyenera kukhulupilira mu chilungamo cha chipulumutso cha Mulungu. Mulungu anakonda ife tonse kwambiri kotero kuti anatipulumutsa kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake pa Mtanda. Pamene tikukhulupilira mu uthenga wabwino umenewu, tinapulumutsidwa ku machimo onse, kumasuka ku chiweruzo ndi kukhala olungama pamaso pa Mulungu. 
“Ambuye, Ndikukhulupilira. Ndine osayenera chipulumutso koma ndikhulupilira mu uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu, kupachikidwa Kwake ndi kuukanso Kwake.” Tiyenera kuthokoza chabe Ambuye chifukwa cha dalitso la uthenga wabwino wa kubadwa mwatsopano. Kukhulupilira mu uthenga wabwino weniweni wa kubadwa mwatsopano ndi chikhulupiliro choona. 
Choonadi cha kubadwa mwatsopano ndi ichi; “Comweco cikhulupiriro cidza ndi mbiri, ndi mbiri idza mwa mau a Kristu.” (Aroma 10:17). “Ndipo mudzazindikira coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani.” (Yohane 8:32). Tiyenera kudziwa choonadi bwinobwino, ndipo tiyenera kukhulupilira m’madzi, mwazi ndi Mzimu umene umapatsa umboni kwa iwo. (1 Yohane 5:5-8). 
“Ndipo coonadi chidzakumasulani.” Awa ndi mawu a Yesu onena za madzi ndi mwazi. Kodi munamasulidwa? Kodi ndife achipembedzo kapena achikhulupiliro? Yesu akufuna okhao amene ali ndi chikhulupiliro cha kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. 
Ngati mukhulupilira mu uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake, ndinu opanda chimo mu mtima mwanu. Komabe, ngati mukhulupilira mwa Yesu mwachabe ngati mbali ya chipembedzo, mukukhalabe mu uchimo chifukwa mulibe chikhulupiliro chanthunthu mu chipulumutso cha Yesu. Anthu a chipembezo amayesa kupeza chiombolo cha machimo awo nthawi-zonse pamene akupemphera mapemphero a kulapa. 
Motero, anthu otere sangapulumutsidwe ku machimo awo kwanthunthu. Ngakhale kuti analapa kwa moyo wawo onse, sikungasinthanitse chikhululukiro chonse cha machimo kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi imfa Yake ya pa Mtanda. Tiyeni tipulumutsidwe mwa kukhulupilira mu uthenga wabwino wa Yesu, umene unatsuka machimo onse a dziko, ngakhalenso aja a mtsogolo. 
Ndikukuuzaniso kuti kulapa masiku onse sikungasinthanitse uthenga wabwino wa kubadwa mwatsopano. Akristu onse ayenera tsopano kukhulupilira mu chikhululukiro cha machimo kudzera mu uthenga wabwino wa kubadwa mwatsopano. 
Sitingalape machimo athu kwanthunthu. Kulapa kwabodza sikungatsogolere munthu kwa Mulungu, koma kutsitsimula chabe moyo wake. Kulapa kwabodza ndi kuulula kwa mbali-imodzi kumene sikuwerengedwa ku chifuno cha Mulungu. Ichi sichinthu chimene Mulungu amayembekezera kwa ife. 
Kodi kulapa koona ndi kotani? Ndi kubwerera kwa Mulungu. Kubwerera ku mawu a chipulumutso a Yesu ndi kukhulupilira m’mawu monga analembedwera. Uthenga wabwino umene umapulumutsa ife ndi uthenga wa ubatizo wa Yesu, kupachikidwa Kwake ndi kuukanso Kwake. Pamene takhulupilira mu uthenga wabwino umenewu kwanthunthu, ndife ndiyeno opulumutsidwa ndi kupeza moyo osatha. 
Iyi ndi nzeru ya uthenga wabwino wa kubadwa mwatsopano; ndi kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake ndi uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu umene unalola ife kubadwanso mwatsopano. 
Pamene Yesu akutiuza kuti tiyenera kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu, anatanthauza kuti tiyenera kubadwa mwatsopano mwa kukhulupilira mu ubatizo wake ndi mwazi wake pa Mtanda. Ndiyeno tidzatha kulowa ndi kukhala mu Ufumu wa Mulungu. Tiyenera kukhulupilira m’mawu Ake. Zinthu ziwiri zimene zikuchitira umboni wa chikhululukiro cha machimo athu, ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake pa Mtanda, ndi mawu amene amatilola ife kubadwa mwatsopano. 
Kodi mukukhulupilira tsopano mu uthenga wabwino wa kubadwa mwatsopano, ndi chikhululukiro cha machimo? Chikhulupiliro mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake pa Mtanda unapulumutsa ife ku machimo a dziko. Tingakhale obadwa mwatsopano ndi chikhulupiliro chimenechi. Popeza Baibulo limatiuza kuti Yesu anatsuka machimo a ochimwa onse m’dziko, n’chifukwa chiani sitiyenera kukhulupilira ndi kubadwanso mwatsopano? 
Iwo amene akhulupilira mu zinthu ziwiri zimene zikuchitira umboni ku kubadwa mwatsopano, ubatizo wa Yesu ndi kupachikidwa Kwake, ndi obadwadi mwatsopano. Ndipo iye amene akhulupilira mwa Mwana wa Mulungu ali ndi umboni mwa iyeyekha (1 Yohane 5:3-10). Pamene mukhulupilira mwa Yesu, simuyenera kusiya uthenga wabwino wa madzi, mwazi ndi Mzimu. 
Monga msilikali Namani anatsukidwa pa Yordano kasanu ndi kawiri kuti achiritsidwe kwanthuthu ku khate (2 Mafumu 5), Tiyenera kukhulupilira kuti Yesu anatsuka machimo onse a dziko kamodzi kokha pa Yordano ndipo mwa ichi anatipatsa chipulumutso chosatha. 
Chifukwa chakuti Yesu anatikonda ife, tingapulumutsidwe ku machimo onse a dziko ndi kukhala ndi moyo osatha mwa kukhulupilira mu uthenga wabwino wa kukhululukidwa ku uchimo. Tiyeni tonse tikhulupilire mu uthenga wabwino wa kubadwa mwatsopano ndi kupeza chipulumutso cha Mulungu.