(Yesaya 28:13-14)“Cifukwa cace mau a Yehova adzakhala kwa iwo langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang’ono, uko pang’ono; kuti ayende ndi kugwa cambuyo, ndi kutyoka, ndi kukodwa mumsampha, ndi kugwidwa. Cifukwa cace imvani mau a Yehova, inu amuna amnyozo, olamulira anthu awa a m’Yerusalemu.”
MPATUKO WA M’BAIBULO
Kodi Baibulo litchula motani mawu akuti “mpatuko?”
Baibulo limatchula wa mpatuko ngati munthu amene ali ndi uchimo mu mtima mwake ngakhale kuti akhulupilira mwa Yesu
Kuli onyenga ambirimbiri olemba nkhani masiku ano, makamaka mu maiko amene ndi osauka. Amaoneka ngati ndi olemba nkhani koma nthawi zambiri amatenga ndalama ku okhudzidwa, kuwaopseza kuti awaulula zimene okhudzidwawo achita. Mawu akuti chinyengo akutanthauza chinthu chimene chikuoneka ngati chenicheni koma sichinthu chenicheni. M’mawu ena, chikusonyeza chinthu chimene zoona zake ndi zosiyana kwambiri ndi kaonekedwe kake kakunja.
Mawu akuti “mpatuko” ndiponso “chinyengo” amagwiritsidwa ntchito pafupi pafupi, makamaka m’mipingo ya ChiKristu.
Pali matanthauzo ooneka ochepa okhudza zimene “wampatuko” amatanthauza ndiponso tanthauzo la “kunama,” kapena pali ena amene akuphunzitsa malingaliro amenewa mogwirizana ndi Baibulo.
Pansi pa zochitika zimenezi, Ndakhudzidwa kuti ndiulule m’mene Baibulo limatanthauzira monga “mpatuko” ndi kuunikira kwambiri pa nkhani imeneyi. Ndikufunanso kufotokoza zitsanzo za mpatuko mu umoyo wa masiku onse ndiponso kulola ife kuti tiganizepo bwino pamodzi. Aliyense amene akhulupilira mwa Mulungu ayenera kuganiza za mpatuko kamodzi kokha pa miyoyo yawo.
Tito 3:10-11 akutanthauzira wampatuko ngati munthu wopatukira chikhulupiliro amene wasandulika konse nachimwa nakhala odzitsutsa yekha. Wampatuko ndi munthu amene akudzitsutsa yekha nakhala ochimwa. Motero iwo amene akhulupilira mwa Yesu koma ali ndi uchimo m’mitima yawo ndi ampatuko pamaso pa Mulungu.
Yesu anachotsa machimo onse kudzera mu ubatizo Wake. Koma ampatuko anakana kukhulupilira mu uthenga wabwino weniweni umene ukubweretsa chipulumutso kwa ochimwa ndipo motero amadzitsutsa okha ndi kukhala m’mipando yauchimo.
Kodi ndinu opatukira chikhulupiliro? Tiyenera kuganiza za zimenechi ngati tikufuna kukhala ndi umoyo wabwino ndi umoyo wachikhulupiliro.
Kodi inu simudzitsutsa nokha kukhala ochimwa ngakhale kuti mukukhulupilira mwa Yesu ngati simunamvere uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu? Ngati mumaziona nokha kukhala ochimwa, ndiye kuti mukupanga zolakwa kwa Yesu mwa kuchepetsa chipulumutso Chake cha ngwiro ndi uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Kudzitchula munthu kuti ochimwa pamaso pa Mulungu ndi kuvomereza kuti munthuyo si mwana wa Mulungu. Iwo amene akuulula kwa Yesu, “Ambuye, Ine ndine ochimwa,” ayenera kuyang’ana bwino chikhulupiliro chawo.
Kodi mungakhulupilire bwanji mwa Yesu ndi kupitiliza kunena kuti ndinu ochimwa pamene Yesu anachotsa machimo onse a dziko ndi kupulumutsa inu kwanthunthu ku chiweruzo chosatha? Kodi mukukana bwanji mphatso Yake yaulere ya chipulumutso ndi kuzitchula kuti ochimwa pamene Yesu anachotsa machimo anu onse kudzera mu ubatizo Wake ndipo anaweruzidwa kotheratu pa Mtanda chifukwa cha machimowo?
Anthu otere ndi ampatuko chifukwa amadzipereka okha kukhala ochimwa kuchotsako mawu a Mulungu. Muyenera kudziwa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu kuti mupewe kuchita mpatuko pamaso pa Mulungu.
Aliyense amene akhulupilira mwa Yesu koma ndi osabadwa mwatsopano ndi wampatuko chifukwa akali ndi uchimo mu mtima wake.
Chifukwa Mulungu anachotsa machimo onse a dziko kuphatikizapo a ife tonse, ndife ampatuko pamaso pa Mulungu ngati tikunyalanyaza dalitso limeneli la chipulumutso. Chifukwa Mulungu ndi oyera, ndife ampatuko ngati tikali ndi uchimo m’mitima yathu. Ngati tikufunadi kukhala olungama, tiyenera kukhulupilira mu uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake a pa Mtanda.
CHIYAMBI CHA MPATUKO MU BAIBULO
Kodi chilolezo chofunika kwambiri cha wansembe ndi chiyani?
Ayenera kubadwa mwatsopano
Tiyeni tione pa 1 Mafumu 12:25-26. “Ndipo Yerobiamu anamanga sekemu m’mapiri Efraimu, nakhalamo, namanga Penueli. Ndipo Yerobiamu ananena m’mtima mwace, Ufumuwu udzabwereranso kunyumba ya Davide.” Yerobiamu anali m’modziwa mwa nduna za Solomo. Pamene Solomo anakhala wampatuko m’zaka zake zina, Yerobiamu anaukira mfumu, ndipo mkupita kwa nthawi anakhala mfumu ya mafuko khumi a Israyeli m’nthawi ya Rehabiamu, mwana wa Solomo.
Choyamba chimene chinakhudza kwambiri Yerobiamu pamene anakhala mfumu wa Israyeli chinali chakuti anthu ake angabwerere ku Yuda kumene kunali kachisi.
Motero, anakhala ndi ganizo la kuteteza kuti chimenechi chisachitike. Iye anapanga mafano a golide awiri ku Beteli ndi Dani ndi kulamula anthu ake kuti azilambira izi. 1 mafumu 12:28 anena kuti, “Potero mfumu inakhala upo, anapanga ana a ng’ombe awiri agolidi,.” Imene anaika ku Beteli, ndipo imodzinso anaika ku Dani ndi kuuza anthu ake kuti alambire, ngakhale kuti kuchita tero kunali chimo lalikulu. Iye anasankha ngakhale ansembe kuti azisogolera kupembedza.
“Pambuyo pa ici Yerobiamu sanabwerera pa njira yace yoipa, koma analonganso anthu acabe akhale ansembe a misanje, yense wakufuna yemweyu anampatula akhale wamsembe wa misanje” (1 Mafumu 13:33). Uko kunali kuyamba kwa mpatuko.
Ngakhale tsopano, ampatuko amasankha ansembe aliyense amene adzipereka kuti angagwire ntchito ya Mulungu. Aliyense amene watsiriza sukulu ya maphunziro a Baibulo angakhale mtumiki, otumikira, olalika oyendayenda ndiponso mkulu wampingo ngakhale kuti sanabadwe mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.
Kodi munthu amene sanabadwe mwatsopano angakhale bwanji mtumiki? Ngati munthu otere wasankhidwa, mpingo umene wamusankha umakhala malo amene ampatuko amapangidwa.
Tiyeni tiganizenso za kuyamba kwa mpatuko. Choyamba, Yerobiamu anachotsa mulungu ndi kuikapo zosema zagolide kuti asunge mphamvu zake zandale. Chachiwiri, anakhazikitsa aliyense odzipereka kuti akhale wansembe. M’mawu ena, anakhazikitsa anthu wamba kukhala ansembe. M’chitidwe otere ukupitilirabe kufikira tsopano.
Mbiri ya mpatuko inapitilizabe bwino ngakhale nthawi ya Yerobiamu inapita. Iwo amene sabadwe mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu sayenera kuloledwa kukhala ansembe.
Kodi aliyense amene watsiriza sukulu yake ya Baibulo angakhale mtumiki kapena otumikira? Kodi nkoyenera kwa iwo kutumikira Mulungu posawerengera kuti sanasankhidwe ndi Mulungu? N’zosatheka. Okawo amene adziwika ndi Mulungu ndi amene akuloledwa kukhala atumiki Ake. Iwo amene akudziwika ndi Mulungu ndi amene abadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.
Kunalembedwa mu 1 mafumu 12:25-26 ndiponso 1 mafumu 13 kuti uchimo wa Yerobiamu unaputa mkwiyo wa Mulungu. Tonse tiyenera kudziwa nkhani imeneyi, ndipo ngati wina sakudziwa bwino zimenechi, ayenera kubwereranso ku Baibulo ndi kufufuza.
Ganizani bwino ngati mukuika zosema zagolide m’malo Mulungu mu utumiki wanu. Kodi inu, mwa mpata ulionse, mumaika patsogolo madalitso a dziko kuopa kuti okutsatirani angabwerere ku uthenga wabwino wa kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu?
Kodi mumauza okutsatirani kuti angachire ku matenda awo ngati angakhulupilire mwa Yesu? Kodi mumawauza kuti azadalitsidwa kuchuma? Kodi mumapatsa maudindo iwo amene sanabadwe mwatsopano kukhala atumiki kapena mamembala akuluakulu mu mpingo wanu ndi kunena kuti chipembedzo chanu ndiye chenicheni? Ngati n’chocho, mukupanga chimo ya Yerobiamu pamaso pa Mulungu ndipo mukuputa mkwiyo wa Wake.
AMPATUKO AMALAMBIRA MULUNGU WA ANA ANG’OMBE AGOLIDE
Ngakhale tsopano, kuli opatukira chikhulupiliro amene akulambira ana ang’ombe agolide. Amanena kuti Mulungu anadalitsa Solomo pamene anapereka nsembe zopsereza chikwi kwa Mulungu. I Mafumu 3:3-5 akunena kuti “Ndipo solomo anakondana ndi Yehova, nayenda m’malemba a Davide atate wace; koma anaphora nsembe nafukiza zonunkhira pamisanje. Ndipo mfumu inapita ku Gibeoni kukaphera nsembe kumeneko; popeza msanje waukuru unali kumeneko, solomo anapereka nsembe zopsereza cikwi cimodzi pa guwalo la nsembe. Ku Gibeoni Yehova anaonekera Solomo m’kulota usiku, nati mulungu, Tapempha cimene ndikupatse. ”
Amaba ndalama kwa owatsatira kupitira mu lonjezo lachinyengo la Zopereka zopsereza chikwi za Solomo.” Iwo otsatira opusa akuberedwa ndalama zawo. Ndipo iwo amene akupembedza ana ang’ombe agolide ngati Mulungu wawo akudyeredwa masuku pamutu ndi ndalama zawo, zimene zikugwiritsidwa nchito ngati zopereka zomangira mipingo. Sichifukwa chakuti mpingo wawo ndi waung’ono, koma akufuna kuba ndalama kwa owatsatira awo.
Kukhazikitsa ana ang’ombe agolide kuti mipingo yawo izipembeza kunali kothawira kokha kumene ampatuko anabweretsa kuti abere ndalama kwa iwo. Ife amene tikukhulupilira mwa Mulungu sitiyenera kutengedwa ngati opusa. Ngati mukupereka ndalama zanu kuti mupembeze ana ang’ombe agolide, siziperekedwa kwa Mulungu, koma zimathera m’matumba mwa ansembe achinyengo amene ndi odzala ndi dyera monga Yerobiamu. Simuyenera kugwa m’misampha ya ampatuko otere.
Ndiyeno n’chifukwa chiyani Mulungu anasangala ndi nsembe zopsereza chikwi za Solomo? Chifukwa chakuti Solomo ankadziwa machimo ake, anadziwa kuti anayenera kufa chifukwa cha machimowo ndi kupereka nsembe molingana ndi chikhulupiliro. Anapereka nsembe zopsereza chikwi kusonyeza kuthokoza pa chipulumutso cha Mulungu. Solomo anali kupereka nsembe zopsereza chikwi masiku onse, poganizira za chiombolo cha madzi ndi Mzimu.
Tsopano, muyenera kukumbukira tanthauzo loona la mpatuko kotero kuti musakanyengedwe ndi ansembe onyenga.
IWO AMENE AKUTUMIKIRA POPANDA KUBADWA MWATSOPANO NDI OPATUKIRA CHIKHULUPILIRO
Kodi ampatuko amanena chiyani za kubadwa mwatsopano?
Amanena kuti ndi obadwa mwatsopano a maso mphenya, amaloto, ndi mitundu yosiyanasiyana yamizimu
Pali aja amene akuphunzitsa ena kuti abadwe mwatsopano pamene iwo okha sanabadwe matsopano m’chikhulupiriro. Iwo onse ndi ampatuko. Akuuza ena kuti akubadwe mwatsopano pamene iwo akulephera kubadwanso chifukwa sakudziwa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Ndizoseketsa kwambiri.
Ansembe onyenga akulalikira uthenga wabodza, kusokoneza uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Iwo akuuza anthu kuti azitsuka machimo awo masiku onse.
Iwo amanena kuti, “Pitani kapemphereni m’mapiri, yesani kusala zakudya, ziperekeni nokha ku ntchito za Mulungu, pempherani pakati pa usiku, khalani omvera, perekani ndalama zambiri kuti timange mipingo, koma khala atcheru ndikusamala machimo anu nokha.”
Kamodzi, ndinamvapo munthu akuchitira umboni kuti ndi obadwa mwatsopano. Iye ananena kuti kumaloto, anali chiimire mu mzere ndipo pamene anafika pa iye, Yesu anaitana dzina lake. Iye anati unali umboni wakuti anali obadwa mwatsopano. Koma kodi kuitanidwa kwake kunali koyenera? Yesu sananene motero.
Mu Yohane 3:5, iye anati, “Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu.” Mulungu ananena kuti okhawo amene ndi obadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu ndi amene angakhale wansembe weniweni. Aliyense amene akhulupilira kuti ndi obadwa mwatsopano kudzera m’maloto, zopeka, mimbulu yauzimu, kapena m’mapemphero a kulapa ndi wampatuko.
Masiku ano, anthu ambiri sakukhulupilira mu mawu olembedwa a Mulungu ndipo akusunga ziphunzitso zawo zachipembedzo m’malo mwa kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Iwo amene akukana kulalikira uthenga wabwino wakubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu ndi aKristu-onyenga ndiponso ampatuko.
WOKONZANSO NDI CHIKRISTU CHATSOPANO
Kodi uthenga wabwino weniweni unayamba liti kusakanizana ndi kuonongedwa ndi zipembedzo zina?
Kuyambira pa nthawi imene Mfumu ya aroma Konstantine ananenera za kulamulira Milani mu 313 A.D
Kodi ndi liti pamene chipembezo cha Chikristu chinapangidwa? Kodi ndi liti pamene zipembezo zina monga Pulezibeteliya, Mesodisiti, Aubatizo, Lisireni, Achiyero, ndiponso uthenga wabwino wathunthu unayamba? Kupangidwanso kunayamba zaka mazana asanu apitawo.
AKristu oyambirira anali aja amene ankatsatira Yesu pamene anali padziko lapans. “AKristu” kutanthauza “aja amene akutsatira Kristu.”
Akristu oyambirira anali atumwi ndi ophunzira awo. Atumwi ndi Atate a mpingo anatsatira uthenga wabwino oona kufikira zaka 313 A.D. Komabe, pambuyo pa ulamuliro wa Milani wa ku Konstantino Wamkulu, aKristu ndi Amuna a mitundu ina anayamba kuphatikizana pamodzi. Zotsatira zake zinali zaka Zakuda zimene zinatha zaka zopitilira chikwi (1000).
Patsogolo pake, zaka za m’ma 16 senchari zoyambirira, Martin Luther ananena za Kukonzanso, anati, “Koma munthu wolungama azakhala ndi moyo ndi cikhulupiriro” (Aroma 1:17). Patsogolo pake, pakati pa zaka 1500~1600, Okozanso monga John calvin ndi John Knox anatsogolera zimenezi kuzichotsa mu Ukatolika. Izi ndi m’mene kukonzanso kunathekera .
Kukozanso inali ntchito ya kukhazikitsa mipingo yatsopano yosiyana ndi Mpingo wa Aroma wa Katolika. Okozanso sanayese kupanga zinazake zokana Uchikatolika paokha.
Cholinga chawo sichinali chakuti apititse patsogolo chikhulupiliro cha kubadwanso kwatsopano kwa madzi ndi Mzimu, koma kuti amasuke okha ku chiwawa ndi chinyengo cha Mpingo wa Aroma wa Katolika. Mpingo wa Aroma wa Katolika anatcha chimenechi kukhala kuukira. Zikutanthauza kuti oukira.
Pa nthawi imeneyo, Mpingo wa Aroma wa Katolika unauza anthu kuti agule zosangalatsa, ponena kuti angapereke mizimu ya akufa Kumwamba ngati angagule zosangalatsa ndi ndalama zambiri zotere. Luther sanazindikire kuti Ukatolika unali olakwika. Ankafuna kokha kuyesa kuletsa Mpingo wa Aroma Katolika kugulitsa zosangalatsa kuti apeze ndalama zomangira Mpingo wa St Peter.
Mwa ichi, tingaone mipingo yotaikana yambiri mu Mpingo wa katolika watsopano youkira: ubatizo watiana, mapemphero a kulapa amene akufanana ndi kuulula pansi pa Mpingo wa Aroma wa Katolika, mwambo wachiyero, kudziwika kokha kwa aja amene anamaliza maphunziro a kupembeza monga otumikira, aulemero ndiponso mipingo yodzitukumula. Zonsezi ndi kutaikana kwa Mpingo wa Aroma wa Katolika.
Kuwerenga kuyambira ku kuchiyambi mu zaka za m’ma 1500 zoyambirira, mbiri ya kuukira inakhala zaka mazana asanu (500) okha. Chaka chimenechi ndi chaka cha 481 m’mbiri ya Kukozanso. Simungazindikire kuti Martin Luther anaukira Mpingo wa amai ake zaka 481 zokha zapitazo. Kuukira sukunachite chilichonse choletsa ulamuliro wa achichepere ake. Kukonzanso kwa chiKristu kukupitabe patsogolo. Ndipo kuyenerabe kupitiliza kupita patsogolo.
Komabe, pali chinthu chimodzi tiyenera kuika m’maganizo. Sitiyenera kuiwala kuti okhao amene ndi obadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu ndi amene angalowe mu Ufumu wa Kumwamba. Tiyeneni tilalikire chimenecho! Kodi m’malalika uthenga wabwino wa Yesu, uthenga wabwino wakubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu? Ngati sichoncho, ndiye kuti simuli mtumiki wa Mulungu. Ndi uthenga wabwino wa “kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu” umene mulungu akufuna kuti ife tikhulupilire. Ndi zimene Yesu anaphunzitsa Nikodemo mu Yohane 3.
Kodi Baibulo limangonena za uthenga wabwino wakubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu, kapena likunena zinthu zina monga kugwira ntchito yabwino mumizinda ndi kukhala ndi umoyo oyera? Indedi zimenezo ndi zofunikiranso. Komabe, mungachite zimenezo pambuyo pakuti ndinu obadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Chifuniro cha Mulungu ndi chakuti ife tikhulupilire mu uthenga wabwino.
ZIPHUNZITSO ZA AMPATUKO
Kodi wampatuko ndani?
Iye amene akali ochimwa ngakhale kuti akhulupilira mwa Yesu
Kodi ndi liti pamene chiKristu chonyenga, chikhulupiliro champatuko chinayamba kukula m’dziko?
Anthu a mu Israyeli ankapembeza Mulungu m’modzi kufikira pamene anapatukana kukhala maufumu awiri m’nthawi ya Yerobiamu monga analembera mu 1 Mafumu 12-13. Kuchokera nthawi imeneyo, Yesu asanabwere ku dzikoli, chikhulupiliro champatuko chinayamba kukula. Kulinso opatukira chikhulupiliro ambiri masiku ano.
Baibulo limanena za ziphunzitso zawo za chinyengo mu Yesaya 28 ndi Tito 3:10-11. Baibulo limanena kuti ampatuko ndi iwo amene akhulupilira mwa Yesu koma akali ndi uchimo m’mitima yawo. Aliyense amene ali otero ndi wampatuko.
Ndipo akuphunzitsa kuti, monga analembera mu Yesaya 28:9-10, “Kodi Mulungu adzaphunzitsa yani nzeru? Kodi Iye adzamvetsa yani uthengawo? Iwo amene aletsedwa kuyamwa, nacotsedwa pamabere? Pakuti pali langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang’ono, uko pang’ono.”
Ampatuko amaonjezera langizo ndi langizo, lamulo ndi lamulo. Kodi ichi chikutanthauza chiyani? Chikutanthauza “Khalani ochenjera, khalani ochenjera, khalani ochenjera ndi iwo amene akunena kuti ndi obadwa mwatsopano kudzera mwa chikhulupiliro chawo mwa Yesu.” Amangokuuzani kuti mukhale ochenjera mulimonse m’mene zilili. Amakuuzani kuti musamvere, musapite, kuti mungagwere mu a mpatuko.
Komabe, ngati ali ndi chidaliro kuti chawo ndi chikhulupiliro chenicheni, n’chifukwa chiyani sangakhale kutali ndi iwo amene akunena kuti zikhulupiliro zawo ndi zosiyana ndi mawu a Mulungu? Ndi zomvetsa chisoni kwambiri. Amanena kuti ndi aKristu enieni, koma alibe mawu ogonjetsera chimene amatchula kuti ndi mpatuko. AKristu oona angapambane ampatuko alionse ndi mawu a Mulungu.
Masiku ano, amene akuti ndi aKristu enieni akuitana obadwa mwatsopano kuti “ampatuko” chifukwa chakuti zikhulupiliro zawo ndi zosiyana. Kodi ife tingakhale bwanji ampatuko pamene tikukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu?
Ngati amene akutchedwa ampatuko akulalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, ndi aKristu enieni azoona. Chimodzimodzi, ngati amene akuti ndi aKristu enieni sakulalikira uthenga wa madzi ndi Mzimu, ndi ampatuko.
Kusiyana pakati pa “uKristu weniweni” ndi “mpatuko” kunagona ngati mwina akulalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu kapena ngati mwina akukhulupilira mwa Yesu ndipo ali ndi uchimo mu mitima yawo kapena ai. Kodi iwo angakhale bwanji ampatuko ngati akukhulupilira m’mawu a Mulungu ndipo ndi obadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu?
Kodi ndi mpatuko kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Ake a pa Mtanda ndi kukhala oyeretsedwa kwanthunthu kuuchimo? Kodi ndi “uKristu weniweni” kusakhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu?
Kuli azipembezo ambiri amene achoka ku Baibulo ndipo akunena kuti ndi “aKristu achoonadi.” Akuchoka mu kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu monga anafotokozera mu Baibulo chifukwa akulakira kokha mwazi a pa Mtanda, kukana ubatizo wa Yesu (madzi).
Kodi kusiyana kuli pati pakati pa Mpingo wa Aroma Katolika ndi Mpingo woukira chikatolika masiku ano? Monga m’mene okozanso anaukira Mpingo wa Aroma wa Katolika, monganso m’mene anatulukira mu Mpingo wa Aroma wa Katolika ndi kumanga kuukira, Nafenso tiyenera kuukirana ndi aKristu akhungu komanso ansembe a chinyengo. Pokhapo kutero ndi pamene tingatsegule maso athu ku uthenga wabwino oona, kukhala ndi chikhulupiliro choona, ndi kupulukutsidwa kwanthunthu kudzera ku uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tipewe kukhala ampatuko?
Tiyenera kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.
Baibulo limatiuza kuti okhawo amene akhulupilira mu uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda ndi amene akutsatira chikhulupiliro choona. Yesu ananena motero kwa Nikodemo mu Yohane 3:1-12.
Ampatuko nthawi zonse amauza owatsatira kuti akhale olimba mu chikhulupiliro chawo. Amawauza kuti ayenera kupemphera pakati pausiku ndi kugwira ntchito mwa mphamvu. Kuli ngati kuuza anthu akhungu kuti athamange.
Zilibe kanthu kuti mukupemphera motani, ndi zopanda ntchito ngati simuli obadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Pamene tikunena kuti iwo amene ndi obadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu ndi olungama, ampatuko amatitsutsa ndi Aroma 3:10, “Palibe mmodzi wolungama, inde palibe mmodzi.” Ndi ndime imeneyi, amatsutsa aKristu ngati ampatuko
Mu choona, komabe, ndi iwo amene ndi ampatuko. Tanthauzo loona la ndimeyi silophweka monga ikumvekera. Ampatuko amenewa sanawerenge Baibulo lonse. Mtumwi Paulo ananena kuti mulibe munthu olungama m’dziko. Anangolinganiza ndime m’Chipangano Chakale limene likunena kuti kunalibe aliyense olungama Yesu Kristu asanabwere kuombola mtundu wa anthu ku machimo awo ndi chipulumutso cha Mulungu. Komabe, Iwo amene ndi opulumutsidwa ndi Yesu anakhala olungama.
Tingaone choonadi ngati tingawerenge ndime chonse. Ampatuko amangochenjeza otsatira awo kuti akhale ochenjera ndi iwo amene chikhulupiliro chawo ndi chosiyana ndi chawo. Kuchotsako mipingo imene akuidziwa kuti ndi ya choonadi, amaletsa otsatira awo kuti asapembedze kwina kulikonse. Choncho mpingo wawo sumayesa kupita ku mipingo imene ikulalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Amakhala ogontha ku uthenga wabwino oona ndipo sangabadwe mwatsopano. Izi ndi ziphunzitso za atsogoleri abodza amene akudzutsa ana amuna ndi akazi a ku gehena. Iwo azaweruzidwa ndi Mulungu chifukwa cha ichi. Ampatuko ayenera kubwerera kwa Mulungu.
Kodi ampatuko ndi ndani? Kodi ndi amene anaomboledwa mwa kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, kapena ndi amene akunena kuti akukhulupilira mwa Yesu koma akulephera kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu?
Tito 3:11 akunena kuti iwo amene akhulupilira mwa Yesu koma akukhalabe “Wodzitsutsa yekha” ndi ampatuko.
Amaphunzitsa owatsatira awo kuti asapite ku misonkhano yachibwereza kumene uthenga wabwino akubadwa mwatsopano wa madzi ndi Mzimu ukulalikidwa, kunena kuti ndioopsa. Kodi “aKristu weniweni” angaope bwanji zikhulupiliro zachiwawa? Iwo ndi amatha chifukwa alibe choonadi kumbali yawo. “Pakuti pali langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo.” Ziphunzitso zampatuko zili motero.
Ansembe ampatuko amatenga zochepa za buku ili, zochepa za buku ilo, kuchokera ku mawu a ofufuza mu zolembedwa, kumbiri ya nkhani ndi kusakaniza mu maganizo awo ndi kupanga zonse kumveka zanzeru.
Amakhulupilira kuti owatsatira awo ndi mbuli ndipo akuyesa kuwaphunzitsa ndi ziphunziso zadziko. Mpingo woona ukulalikira mawu a Mulungu ndi kuphunzitsa okhulupilira ndi mawu a Mulungu. Anthu sabwera ku mpingo kuti aphunzitsidwe mu njira za mawu a dziko. M’malo mwake, amabwera ku mpingo kuti amvere zinthu zakumwamba zimene sizingamveke m’dzikoli. Amabwera kudzamvera mawu a Yesu.
Anthu amalowa m’mipingo yawo ngati ochimwa koma amafuna kudzuka mu mpingo ngati okhulupirira amene alibe uchimo. Kodi ansembe ampatuko amawaphunzitsa chiyani? Amauza otsatira awo kuti asamapite ku misonkhano yobwereza kumene atumiki a Mulungu akulalikira uthenga wabwino oona. Amateteza otsatira awo kuti asakhale obadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.
Izi ndi zopusa kwambiri. Angathe kunyenga otsatira awo koma sangathe kunyenga Mulungu.
Kodi ansembe onyenga angapange otsatira awo kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu?
Ai. Okhao obadwa mwatsopano ndi amene Angapange ena kubadwa mwatsopano.
Ampatuko, ngati ndinudi mtumiki wa Mulungu, kodi simumvera Mzimu ukukuyandikira? Muyenera kubwereranso. Muyenera kupewa otsatira anuo osawaletsa kuti asapezeke ku msonkhano obwereza kumene atumiki oona a Mulungu amalalika uthenga wabwino wa kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.
Ampatuko amaphunzitsa otsatira awo ndi zipembezo zokha, choncho pamene akumana ndi zofufuza zina, amagonjetsedwa. Ndi zomvetsa chisoni kwambiri. Ansembe-achinyengo ali bwino pa utumiki opanda mawu a Mulungu. Amalalikira, kufufuza, kutumikira kuchokera ku zilimbikitso zawo zokha. Iwo amene akutumikira ndi kulalikira popanda mawu a Mulungu ndi ampatuko ndiponso ali wolipidwa (Yohane 10:13).
Atumiki onyenga ndi ampatuko chifukwa mkati mwawo ndi kunja kwawo ndi kosiyana. Anthu ena amanena mipingo imene sikuyenera kukhazikitsidwa kukhala zipembezo kuti ndi mipingo yampatuko. Komabe, ina mwa mipingo imeneyo sikufuna kukhala kumbali ya chipembezo chilichonse chifukwa mipingo yambiri ikupezeka kutali kwambiri ndi ziphunzitso zoona za Baibulo.
Ampatuko amauza otsatira awo kuti aomboledwe ngakhale kuti iwo okha sanakonze vuto la machimo awo. Akuchita tchimo wa Yerobiamu. Ngati pali wina aliyense amene adakali ndi uchimo mu mtima mwake koma akuyesa kuchita ntchito za Mulungu, ayenera kuzindikira kuti machimo ake ndi kuyera kwa Mulungu ndi kosayenerana. Ayenera kudziwa kuti ndi wampatuko.
Motero, ngati aliyense amene akulalikira kapena ali ndi udindo mu mpingo akali ochimwa, ayenera kudziwa kuti ndi wampatuko. Iye ndi wampatuko chifukwa sakudziwa uthenga wabwino wa chipulumutso cha Kristu, uthenga wabwino wakubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Ngati munthu waphunzira Baibulo kuchokera kwa ampatuko ndi kuphunzitsa ena m’njira imodzimodzi, amakhalanso wampatuko.
Timadziwa mtengo chifukwa cha zipatso zake. Iwo amene akhala olungama mwa kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake amangobala olungama pamene iwo amene akali ochimwa ali oyenera kubala ochimwa. “Comweco mtengo wabwino uli wonse upatsa zipaso zokoma; koma mtengo wamphuci upatsa zipatso zoipa” (Mateyu 7:17).
KODI ANSEMBE A AMPATUKO AMALALIKIRA CHIYANI MU ULALIKI AWO?
Kodi ansembe ampatuko amalalikira chiyani mu ulaliki wawo?
Zaumulungu za dziko ndi maganizo a munthu
Ansembe onama khalani tcheru ku ichi ndi icho. Kodi n’chifukwa chiyani ali ochenjera motero? Ayenera kukhala ochenjera kuti mabodza awo angavumbulutsidwe chifukwa alibe chikhulupiliro chomveka cha kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.
Ampatuko amatenga pang’ono kuno, ndiponso pang’ono uko. Amanyenga anthu ndipo amaphunzitsa popanda kudziwa tanthauzo lenileni la uthenga wabwino.
“Langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang’ono, uko pang’ono” (Yesaya 28:13).
Lamulo ndi lamulo, iwo amatero, “Mawu awa amatanthauza choncho ndi choncho mu Chihebri komanso choncho ndi choncho mu chiGriki. Ndipo kuli maphunziro otere ndi otere.” Iwo amachenjezanso anthu kukhala atcheru ngati akumana ndi maphunziro a chipulumutso amene akuonetsa khalidwe lapoyera lakuda-ndiponso-loyera. Iwo amati, Martin Luther ananena ichi ndiponso John Calvin ananena icho pamene John Knox ananena chotere ndi chotere, ndipo tikuganiza kuti onse akupanga nzeru m’njira ya iwo okha.”
Iwo sakudziwa zimene akuyankhula kapena zimene iwo akukhulupilira. Iye amene ali ndi chikhulupiliro choona amaonetsa choonadi mu khalidwe lakuda-ndi-loyera. Okhulupilira oona amanena poyera kusiyana pakati pa obadwa mwatsopano ndi iwo amene sanabadwe mwatsopano. Timalalikira uthenga wabwino wa kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu poyera.
Koma ampatuko ali m’dziko lowawa. Chikhulupiliro chawo chili ngati cha mleme. Monga mleme amakonda mkati mwa dzenje nthawi yamasana ndi kutuluka kunja kokha usiku, ampatuko amakonda kupembeza kumeneku, ndipo amakhulupilira ichi ndi icho. Sadziwa kuti choonadi ndi chiyani. Pamene wansembe wa mpatuko wapita ku gehena, otsatira ake amamuperekeza ku malekezero owawa. Anthu ambirimbiri amapita ku gehena chifukwa amakhulupilira mwa aneneri onyenga.
Kodi mtumiki wanu anabadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu? Kodi amalalikira mawu a uthenga wabwino wakubadwa mwatsopano monga analembera mu Baibulo? Ngati amatero, ndinudi amwayi, koma ngati satero, mudzaweruzidwa. Ngati simunabadwe mwatsopano, muyenera kumvera uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, kuwerenga mabuku amene akufotokoza za iyo, ndi kubadwa mwatsopano.
Ampatuko samakonda uthenga wabwino wa kubadwa mwatsopano. Amalalikira kuti, “Yesu Kristu anabwera kuzachotsa machimo athu, ndipo anaterodi. Iye akutsukabe machimo athu lero ndipo adzapitilizabe kuchita choncho mtsogolo.” Kodi izi zingakhale bwanji zoona? Amanena kuti ndi olungama, koma akupitiliza kumachimwa. Amakhala olungama kwa kanthawi ndipo patsogolo pake amakhala ochimwa.
Maphunziro awo ndi olakwika. Ndi zabodza. Aliyense amene ndi olungama tsopano ndi kukhala ochimwa patsogolo pake ndi wampatuko, mneneri wabodza. Aliyense amene adzitsutsa yekha, amene adzinyenga yekha ali chimodzimodzi.
TEMBELERO LA MULUNGU LILI PA OTSATIRA AMPATUKO
Kodi ampatuko amakamira pa chiyani?
Pa ntchito
Ampatuko samadalilika. Motero sangatengere owatsatira awo kukubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu pamene otsatira awo apita kwa iwo ndi kuwafunsa m’mene angabadwire mwatsopano. M’malo mwake, amapatsa otsatira awo ganizo losamveka lakuti anthu angabadwe mwatsopano m’maloto ndiponso sangadziwe kuti ndi liti pamene angabadwe mwatsopano. Uku ndi kusaganiza bwino.
Yesu anati mu Yohane 3, “Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu.” Komabe masiku ano, anthu olungama amene ndi obadwa mwatsopano amatchedwa ampatuko odzitukumula.
Ansembe achinyengo amanena kuti sangaziitane okha olungama chifukwa ndi odzichepetsa. Amauza owatsatira, “musapezeke pa msonkhano ulionse wachiyanjano kumene mlaliki akufuna kulalikira za dalitso la kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Ngati ndinu obadwa mwatsopano, muzakhala ampatuko. Mudzaweruzidwa ndi mpingo umenewu. Ngati mukufuna kukhala nafe, khalani ochimwa, ndipo Mulungu azakupangani kukhala olungama pamene nthawi idzakwane.” Icho ndi chimene akunena. Chimene akutanthauza kwenikweni ndi chakuti ndi kufuna kwanu kusankha kubadwa mwatsopano kapena ai.
Ampatuko amauza otsatira awo, “Muyenera kukhala ndi ife, koma kubadwa mwatsopano ndi mbali yanu. Choncho, yesani pa inu nokha. Khalani choncho m’mene mulili tsopano, ndi kupita pamaso pa Mulungu nthawi ikakwana, ndiyeno mudzapeza choonadi. Sindikudziwa chimene chidzachitika pambuyo pa izo. Koma uwu ndi mpingo wa choonadi, choncho muyenera kukhala ndi ife.” Kodi muganiza kuti izi ndi zoona?
Awa ansembe ampatuko amatenga pang’ono pano ndiponso pang’ono apo ndi kupanga maphunziro awo. Ndiyeno chimakhala choonadi chawo chokha. Iwo sakudziwa za mawu a Mulungu amene akunena za madzi ndi Mzimu.
Ampatuko amatanthauzira Baibulo kulingana ndi maganizo awo. Tiyenera kutanthauzira Baibulo mogwirizana ndi mawu onenedwa, koma iwo amatanthauzira m’njira yawo. Ndi chifukwa chake kuli azipembezo ambiri ndiponso zipembedzo zochuluka mu Chikristu.
Chifukwa chakuti kuli zipembezo zampatuko zambiri ndi opembeza ampatuko, kuli mabuku ampatuko osawerengeka. Ansembe Onama amatengamo pang’ono m’buku ili ndiponso pang’ono m’buku ilo pamene akulalikira. Ansembe oona komabe, amalalikira kuchokera m’Baibulo mokha.
Ampatuko amaba ndi ndalama za otsatira awo m’njira zochenjera kwambiri. Iwo amadya ndi kukhala bwino m’dzikoli ndi kupita ku gehena chifukwa analephera kubadwa mwatsopano. Ichi ndi chimaliziro chimene Mulungu wakonzekera iwo.
Mulungu anapilira nawo poyamba. Koma kwa iwo amene akukana mokhazikika kuti alole dalitso la kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu, Iye adzawatumiza ku gehena.
Mulungu adzaweruza ampatuko. Ampatuko amakhulupilira mwa Mulungu molimba ndipo amakhala ndi makaundula ambiri a zonenera za Baibulo ndi ntchito zaumulungu poyambirira. Koma pang’ono ndi pang’ono, amayamba kulalikira pa lamulo la munthu, kotero kuti otsatira awo asabadwe mwatsopano.
Ampatuko amakakamira kwambiri pa ntchito zawo za dziko lapansi. Mtumiki aliyense amene sakulalikira uthenga wabwino wa kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu ndi wampatuko pamaso pa Mulungu.
Amakakamiza otsatira awo mpaka kumapeto. Amawakakamiza kuti azipezeka ku mapemphero ausiku masiku- makumi anayi (40), masiku- zana (100) mapemphero a m’mawa kwambiri, mapemphero a kuphiri, kusala chakudya pafupi pafupi, kupanga misonkho yomangira mipingo, nsembe zopsereza chikwi, zopereka za misonkhano yachiyanjano…ndi zina zotere. Amapanga ngakhale zithunzi zoonetsa okhulupilira aliyense m’mene waperekera. Pongoyang’ana zipatso za ntchito zawo, tingaone kuti ndi ampatuko.
Tembelero la Mulungu ligwera otsatira awonso. Otumikira amene akulalikira popanda kubadwa mwatsopano ndi otsatira awo onse ali pansi pa temberero la Mulungu.
AMPATUKO AKUYESA KUWERENGA MAGANIZO A OWATSATIRA AWO
Kodi n’ chifukwa chiyani ampatuko akufuna kuwerenga maganizo a owatsatira awo
Chifukwa sanabadwe mwatsopano, koma akutumikira mwa chinyengo komanso popanda Mzimu m’mitima yawo.
Ansembe ampatuko amalira masiku onse. Amaonetsetsa kuti akukondweretsa madikoni aakulu ndi madikoni aakazi, akulu ampingo, madikoni wamba ngakhale anthu wamba. Ndi m’mene akukhalira masiku onse.
Amachita ngati achinyengo masiku onse. “woyera ndi wachifundo....” Ali odzala ndi uchimo koma amayenera kunena zinthu zachiyero. Choncho amakhala achinyengo mwathunthu tsiku lililonse.
Olalika nthawi ina ananena kuti, “Ndi tembelero kutumikira popanda Mzimu mkati.” Chimene ichi chikutanthauza ndi chakuti ndi mpatuko kugwira ntchito ya Mulungu popanda kuomboledwa; ndi moyo otembeleredwa. Ngati ndinu m’modzi wa ampatuko, muyenera kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.
Aliyense amene akhulupilira mwa Yesu koma sanabadwe mwatsopano ndi wampatuko. Kuonjezera pa chimenechi, aliyense ayenera kubwerera ku uthenga wabwino wa kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Olungama okha amene ndi obadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu ndi amene angalalikire uthenga wabwino kwa ena.
AMPATUKO AMALILIRA MTENDERE BASI
Kodi ansembe ampatuko amakhutilitsa motani otsatira awo?
Iwo nthawi zonse amalilira mtendere, kunena kuti otsatira awo angalowe mu ufumu wa Kumwamba ngakhale kuti ndi ochimwa.
Yesaya 28:14-15 says, “Cifukwa cace imvani mau a Yehova, inu amuna amnyonzo, olamulira anthu awa a m’Yerusalemu. Cifukwa inu munati, ife tapangana pangano ndi imfa, tabvomerezana ndi kunsi kwa manda; pakuti mliri wosefukira sudzatifikira ife; pakuti tayesa mabodza pothawirapo pathu, ndi kubisala m’zonyenga”
Kodi anthu amnyozo ndani pano? Ndi iwo amene akulalikira mawu a Mulungu, ndi kusakaniza ndi zikhulupiliro zawo zolakwika. Mulimonse m’mene maganizo a olalikira alili, zilizonse zimene a zaumulungu akunena, ayenera kupereka tanthauzo lenileni la Baibulo. Koma ansembe ampatuko akulalikira Baibulo m’njira imene akuiona kuti ndi yoyenera kwa iwo. Awa ndi anthu amnyozo.
“Ife tapangana pangano ndi imfa, tabvomerezana ndi kunsi kwa manda; pakuti mliri wosefukira sudzatifikira ife.”
Ampatuko amanena kuti mliri sudzawafikira pa iwo. Amauza anthu kuti asade nkhawa. Chionongeko ndi gehena zikuwayembekezera, koma amanena kuti musade nkhawa, chionongeko ndi gehena sizipezeka chifukwa cha iwo. Choncho muyenera kukhala kutali ndi ampatuko otere ngati mukufuna kuti mukhale ndi moyo.
Ampatuko amanena kuti simuyenera kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Kodi ndi zoona? Ai, n’zosatheka. Simungalowe mu ufumu wa Kumwamba ngati simuli obadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.
Kodi ndikoyenera kusalowa mu ufumu wa Kumwamba? Uku ndi chimodzimodzi ndi kufunsa kuti ngati ndi koyenera kupsya ku gehena. Nzopanda ntchito kunena kuti, yankho ya mafunso onse ndi ai. Tiyeni tonse tikhulupilire mu uthenga wabwino wa kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu ndi kulowa mu ufumu wa Kumwamba pamodzi.
Ansembe ampatuko amanyenga anthu, ponena kuti chifukwa akukhulupilira mwa Yesu, kuli koyenera kwa iwo kukhalabe ochimwa ndi kuti sadzapita ku gehena.
Kodi Yesu amakusamalirani ngakhale kuti ndinu ochimwa? Kodi ochimwa angapite Kumwamba? Kodi mungapewe kupita ku gehena ngakhale kuti ndinu ochimwa? Kodi zinalembedwa M’baibulo kuti simuyenera kupita ku gehena ngati mukhulupilira mwa Yesu, ngakahle kuti muli ndi uchimo mu mtima wanu?
Ampatuko, amanena kuti anapangana pangano ndi imfa, kotero kuti imfa sidzabwera kwa iwo. Amanena kuti okhulupirika angapewe kuweruzidwa ku gehena ngakhale kuti iye ali ndi uchimo mu mtima wake. Kodi muganiza kuti zimachitika m’njira imeneyi?
Ampatuko amakopa anthu ndi chilimbikitso, ponena kuti imfa ndi gehena sizikuwayembekezera. Ansembe ampatuko amasankha iwo amene sanabadwe mwatsopano kukhala ma dikoni, akulu ampingo, atumiki. Koma ayenera kudziwa kuti onse adzapita ku gehena chifukwa sakukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Zimene ayenera kuchita ndi kuika mwa otsatira awo chikhulupiliro cha uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Kodi okhulupilira, ngakhale kuti ndi ochimwa, ndi oyenerabe kulowa Kumwamba? Kodi ochimwa angapite Kumwamba? Kodi Baibulo imanena kuti ochimwa amapita Kumwamba? Ai. Kodi kuli munthu olungama amene ndi uchimo? Ai. Izi ndi ziphunzitso za ampatuko ndiponso a zamulungu-onyenga.
Baibulo limanena kuti, “Pakuti mphotho yace ya ucimo ndi imfa” (Aroma 6:23). Ndi lamulo la Mulungu. Iye amapereka ochimwa onse molunjika ku gehena. Mosiyana ndi tsoka loopsya limeneli, komabe, onse amene ndi obadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu ndi olandiridwa Kumwamba.
“Pakuti mliri wosefukira sudzatifikira ife; pakuti tayesa mabodza pothawirapo pathu, ndi kubisala m’zonyenga.” Ansembe onyanga amanena mawu okhudza zimenezo ndipo molimba amakhulupilira kuti sadzapita ku gehena ngakhale kuti ali ndi machimo m’mitima yawo. Chifukwa akubisala kuseli kwa bodza ndiponso m’zonyenga, Mulungu sangachite chilichonse chowathandiza. Amakhulupilira m’zonyenga zawo zokha. Chifukwa akukhulupilira m’zonyenga zawo m’malo mwa mawu a Mulungu, iwo ndi ampatuko ndiponso ochimwa oyenera ku gehena. Kodi ndi chokalipitsa kotani kuti ndi ambiri a iwo.
AMPATUKO AMAKONDWERA MU NDALAMA ZOKHA BASI
Kodi cholinga cha ansembe ampatuko ndi chiani?
Ndi kupeza ndalama zambiri kuchoka kwa otsatira awo.
Ampatuko ndi ansembe onyenga amakonda ndalama zokha. Iwo ndi osilira. “Kodi ndi ndalama zingati zimene munthu uyu adzapereka ngati angabwere ku mpingo wanga?” Amaganizira za chakhumi chimene adzapereka. Uku kuli ngati kupembeza mwana wa ng’ombe wa golide. “Chonde ndiloleni ndikhale ochita bwino, ndiloleni ndipange ndalama zambiri, Ambuye.” Ansembe onama amaphunzitsa anthu kuti azipemphera motero.
Iwo amati, “Ngati mukukhulupilira mwa Yesu, muzapanga ndalama zambiri, muzabala pamene muli osabala, muzapambana mu malonda anu.”
Anthu ambiri akunyengedwa ndi ansembe a onama amenewa, ndipo akuberedwa ndi ndalama zawo ndiponso akupita ku gehena chifukwa cha mabvuto awo. Izi ndi zopanda chilungamo bwanji! Ngati munthu wina wakhala pansi ndi kuganizira zachinyengo za ampatuko wabwera mu nzeru zake, adzadabwa kuona kuti ndi ndalama zingati zimene wapereka kwa onyenga ake. Adzadzikwiyitsa yekha ku zopusa zake pa kutsatira ndi kugwirira nchito onyengawo.
Ampatuko amakonda kwambiri zinthu zimene amaona ngati ndi lamulo la chipembezo. Otsatira awo amazipereka okha ku mapemphero a m’mawa, mapemphero a ku phiri, zopereka zapadera, chakhumi, zopereka za pa mlungu. Pali zifukwa zambiri zotengera ndalama kwa otsatira awo.
Otsatira awo amagwira ntchito molimbika, koma akali ndi uchimo m’mitima yawo chifukwa palibe amene anawaphunzitsa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Ena amawafunsa za iwo, koma sakutengapo yankho lolondola. Aliyense amene ndi sanabadwe mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu ndi wampatuko.
AMPATUKO OMVETSA CHISONI PAMODZI NDI OWATSATIRA AWO
Kodi n’ndani omvetsa chisoni kwambiri m’dziko?
Iwo amene akutumikira popanda kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu
“Oho inu ampatuko omvetsa chisoni! Muyenera kugwira ntchito pa chiombolo chanu poyamba!” Chizindikiro chachikulu cha chikhulupiliro cha abodza ndi kulambira ana ang’ombe agolide a Yerobiamu. Chinthu choyamba chimene ampatuko anachita m’nthawi ya Chipangano cha Kale ndi kumanga kachisi ndi kuikamo ana ang’ombe agolide (1 Mafumu 12:25-33).
Masiku ano, amamanga mipingo ikuluikulu ndi kubera ndalama otsatira awo. Iwo amauza otsatira awo kuti atenge ngongole ku ma banki kuti apereke za kumangira mpingo waukulu. Iwo amagwira ntchito yotengera mpingo ndi kupititsa mbale zotengelamo. Ndalama, mphete, nkholoko za golide zimadzadza mbale nthawi yochepa. Ampatuko amagwira ntchito mwa njira imeneyi. Ndi chimodzimodzi mu mipingo yonse ya ampatuko.
Kunja, amaoneka ngati akufuna zinthu za uzimu, koma poyera akufuna ndalama zokha. Ndikukuchenjezani kuti mutalikirane nayo mipingo imene imasamalira za ndalama zokha. Chonde musapite ku mipingo kumene olemera okha ndi amene akulandiridwa bwino. Ndi kulakwitsa kulengeza kuchuluka kwa zopereka za mpingo chifukwa amachita choncho ndi chiyembekezo cha kupeza ndalama zambiri.
Ampatuko amanena mawu achikoka kwa owatsatira awo.
“Mudzadalitsidwa ngati mukhulupilira mwa Yesu.”
“Dziperekeni nokha ku nchito ya Mulungu. Pamene mukuchita kwambiri, ndi m’mene madalitso anu adzakhalira.”
“Ngati mukugwira nchito ya ukulu mpingo, muzadalitsidwa mu zinthu zambiri.”
Mwa ichi, otsatira awo amalimbirana okha kuti akhale akulu mpingo. Ngati kunalibe malipiro alionse, ndani akanafuna kutumikira ngati mkulu mpingo? Ndipo akulu mpingo naonso akufunika kupereka ndalama.
Kodi amasankhidwa kuchokera m’mene akukhulupilira mu chiphunzitso cha chipembezo, kapena m’mene alili achangu kwambiri ku gulu ndipo ndi ndalama zingati zimene apereka ku mpingo? Ndi zoona.
Ampatuko amasamala za ndalama zokha. Iwo akufuna a kumanga mipingo ikuluikulu basi. Iwo sasamala ngati otsatira wawo wapiti ku gehena malinga ngati apereka ndalama zambiri.
Ampatuko ndi aja amene akugwira ntchito ya mkate. Amatchera anthu awo ndi maudindo apamwamba. Amapereka maudindo kwa otsatira awo mwachisawawa (Ezekieli 13:17-19). Izi zikutanthauza kuwamangilira ku mpingo wawo ndi kuchulukitsa chuma chake. Ampatuko samalalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Iwo amangoyesa kuzilemeletsa okha.
Ngakhale munthu amene wapezekapo pa mpingo kwa miyezi yochepa angakhale dikoni, Kuonjezerapo, ngati ndi ochita bwino ndi chiphunzitso ndi mbiri ya chuma, amakwezedwa kukhala mkulu mpingo. Izi zonse ndi mwambo wochititsa manyazi wa uchimo wa Yerobiamu, amene anaika ng’ombe ya golide m’malo mwa Mulungu.
Ampatuko amalambira ana ang’ombe agolide. Iwo samathandiza anthu awo kukhala obadwa mwatsopano. Iwo amangotenga ndalama kwa otsatira awo mwa kuwanyengerera ndi malonjezo a madalitso a dziko. Iwo samasamala za otsatira awo kuti akuweruzidwa ku gehena malinga ngati mpingo wawo ukumveka kuti uli ndi chuma.
AMPATUKO AKUSOWA CHITSIMIKIZO MU ULALIKI AWO
Ampatuko amakonda kunena kuti “kapena” kapenanso “mwina” mobwereza bwereza chifukwa amasowa zenizeni mu zimene akunena. Iwo alibe chikhulupiliro m’mawu a Mulungu ndipo sakukhulupilira moona mu zimene akulalikira. Ndondomeko ya chikhulupiliro chawo sichigona mkati mwa chikhulupiliro mu mawu a Mulungu. Iwo amanena kuti, “Mwina kunanenedwa kuti…” Iwo samanena poyera ndi chilimbikitso. Kukanakhala bwino kuti sanaphunzitse otsatira awo chilichonse m’malo mwa kuwaphunzitsa zabodza.
Ampatuko sangatsogolere anthu mu kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Amangoweruzira anthu ambiri ku gehena.
AMPATUKO AMATENGA MBALI YA ANENERI ONYENGA
Kodi n‘chiyani chikukhazikitsa kunyozera Mzimu?
Kukhulupilira mwa Yesu pamene akukhala ngati ochimwa posakhulupilira mu ubatizo Wake
Mateyu 7 akutiuza za iwo amene akhulupilira mwa Yesu koma akupitabe ku gehena. Ampatuko adzalilira kwa Mulungu pa tsiku lomaliza. Monga analembera mu Baibulo, “Ambiri adzati kwa ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mau m’dzina lanu, ndi m’dzina lanunso kuturutsa mizimu yoipa, ndi kucita m’dzina lanunso zamphamvu zambiri? Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziwani inu nthawi zonse; cokani kwa Ine, inu akucita kusayeruzika.” (Mateyu 7:22-23).
Iwo sakhulupilira kuti Yesu anatsuka machimo onse a munthu; samakhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Iwo amachita kusayeruzika. Kodi izi zikutanthauzanji? zikutanthauza kuti akuuza anthu kuti azikhulupilira mwa Yesu pamene akali ndi uchimo m’mitima yawo. Mungadenkhawa kuti ndichiyani cholakwika ndi chimenechi koma ndi chimo lalikulu kwa Mulungu.
Pamene ochimwa akulalikira kwa anthu ena kufunika kwa kukhulupilira mwa Yesu, sangawatsogolere ku kubadwa mwatsopano chifukwa iye mwini anali sanabadwe mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Motero ampatuko amangobala ochimwa amene amakhulupilira mwa Yesu. Ndi kuchimwira Mzimu kuchita kusayeruzika.
Ampatuko samakhulupilira m’mawu a Mulungu kapena kulalikira uthenga monga unalembedwera. Iwo amangoba ndalama kuchoka kwa otsatira awo. Ndi ochimwa ngakhale kuti akukhulupilira mwa Yesu. Akuyesa kutsogolera ena pamene nawonso sanabadwe mwatsopano iwo okha. Mwa njira imeneyi, amachita kusayeruzika.
AMPATUKO SI ENA KOMA OTSANZIRA A OLUNGAMA
Kodi tingasiyanitse motani pakati pa aja amene anabadwa mwatsopano ndi aja amene sanabadwenso?
Tingasiyanitse mwa kuyesa ngati ali ndi uchimo kapena ai.
Musanyengedwe ndi alaliki abodza amene amanena kuti ndi ochimwa. Musawapatse ndalama zanu. Musawapatse ndalama zimene-mwavutikira popeza kwa ochimwa amenewo.
Kodi n’chifukwa chiyani mukupereka ndalama kwa olalika aja amene sangakuthandize inu ku machimo anu? Ngati mukufuna kupereka ndalama ku mpingo, yembekezani kufikira machimo anu atachotsedwa kudzera mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Monga muli okopera mu zaluso, mulinso okopera mu umoyo. Alipo, mwachitsanzo, mipingo yokopera imene simatha kutsuka machimo onse a mu mtima. Kodi mungadziwe bwanji chipembezo chokopera? Kukopera ndi chinthu chimene chikuoneka chenicheni kunja koma mwachoona ndi chosiyana mu chinthu chenicheni.
Muyenera kusankha pa inu nokha. Kodi alaliki oona ndi otani? Kodi ampatuko ndi otani? Kodi chikhulupiliro cheni cheni ndi chotani? Okhulupilira eni eni ndi amene akukhulupilira mwa Yesu ndi mpamvu Yake yachiombolo. Iwo alibe uchimo mu mitima yawo. Koma ampatuko ali ndi uchimo mu mitima yawo. .
Kodi anthu onse ali monga awa ampatuko? Zingakhale choncho. Komabe, tiyeni tibwerere ku Baibulo. Aliyense amene akhulupilira mwa Yesu ndipo sanabadwe mwatsopano ndi wampatuko. Ndi za poyera kuti obadwa mwatsopano ndi okhulupilira enieni. Motero, iwo amene sanabadwe mwatsopano ndi ampatuko. Ampatuko ndi aja amene akhulupilira mwa Yesu koma akali ndi uchimo m’mitima yawo.
Ampatuko ndi okopera kwa olungama. Ayenera kudziwa kuti njira yakukhala oyeretsedwa ndi kukhulupilira mwa Yesu koma mwatsoka akali ndi uchimo m’mitima yawo. Iwo amadzikhulupilira okha kuti ndi ochimwa. Amanena kuti angapitebe Kumwamba ndipo amanena kuti amalambira Mulungu. Zikumveka kwambiri ngati ndi olungama, koma tiyeni osati tinyengedwe ndi okopera.
CHIWERUZO CHA MULUNGU CHIKUYEMBEKEZA AMPATUKO
Kodi chifukwa n’chiyani uthenga wabwino unasinthidwa?
Chifuka chakuti ansembe abodza ndi ampatuko anasakaniza zikhulupliro za anthu zolakwika ndi uthenga wabwino.
“Cifukwa cace Yehova ati, Yehova wa makamu wamphamvu wa Israyeli, Ha! Ndidzatonthoza mtima wanga pocotsa ondibvuta, ndi kubwezera cilango adani anga; ndipo ndidzaikanso dzanja langa pa iwe, ndi kukusungunula kukusiyanitsa iwe ndi mphala yako, ndipo ndidzacotsa seta wako wonse: ndidzabweza oweruza ako monga poyamba, ndi aphungu ako monga paciyambi; pambuyo pace udzacedwa mudzi wolungama, mudzi wokhulupirika. Ziyoni adzaomboledwa ndi ciweruzo, ndi otembenuka mtima ace ndi cilungamo. Koma kupasula kwa olakwa ndi kwa ocimwa kudzakhala kumodzi, ndi iwo amene asiya Yehova adzathedwa. Cifukwa adzakhala ndi manyazi, cifukwa ca mitengo yathundu munaikhumba, ndipo inu mudzagwa nkhope, cifukwa ca minda imene mwaisankha. Cifukwa mudzakhala ngati mtengo wathundu, umene tsamba lace linyala, ngatinso munda wopanda madzi. Ndimo wamphamvu adzakhala ngati cingwe cabwazi,ndi nchito yace ngati nthenthe; ndipo zonse zidzayaka moto pamodzi, opanda wozimitsa.” (Yesaya 1:24-31).
Mulungu akutiuza kuti ngati tingakhulupilire mwa munthu, tizamva chisoni chifukwa cha munthu. Iye anatiuza kuti tizakhala ndi chisoni chifukwa cha mpingo umene tinasankha tokha, ndipo chisoni chimenechi chizakhala ngati mtengo umene masamba ake azimiririka ngati dimba limene lilibe madzi.
Iye akutiuza kuti ansembe abodza ndi otsatira awo amene akhulupilira mwa lamulo la munthu m’malo mwa mawu a Mulungu adzakhala chopinga ndipo ntchito zawo izaonekera. Onse adzapsya mu gehena. Alaliki abodza ndi ampatuko amene asanaomboledwe komanso ochimwa ndi adani a olungama adzaweruzidwa ndi lawi la Mulungu.
Mipingo yomangidwa mwa maphunziro azamulungu okha amaoneka bwino kunja, koma ndiopanda kanthu mkati. Mpingo ulionse umene sukupezeka pa chikhulupiliro cha mawu a Mulungu ndi uthenga wabwino wa kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu uli ngati dimba limene lilibe madzi.
Ingakhale mtengo, koma ndi mtengo wakufa umene ukulephera kubala chipatso. Pamene chitsime chikhala chilibe madzi, sichikhalanso chitsime.
“Ndimo wamphamvu adzakhala ngati cingwe cabwazi, ndi nchito yace ngati nthenthe; ndipo zonse zidzayaka moto pamodzi, opanda wozimitsa.” Iwo amene alibe Mzimu angaoneke olimba kwa ena, koma m’maso mwa Mulungu, alingati chopinga chomangidwa ku moto wa ku gehena.
Ambuye anafunsa, “Mlonda, nthawi yanji ya usiku?” (Yesaya 21:11) Olungama amene ali ndi umoyo wosatha ayenera kulalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu pakati pa usiku.
Mulungu ndi kuunika ndipo Satana ndi mdima. Mulungu amatsogolera anthu ku chilungamo ndipo Satana amatsogolera anthu ku makachisi onama a zowawa ndi zaumulungu zonyenga.
Mu nthawi ya mneneri Yesaya, chikhulupiliro cha anthu chinali chowawa monga m’mene chilili tsopano. Iwo anasakaniza mawu a Mulungu ndi zaumulungu onyenga ndi ulamuliro wa anthu a dziko. Anasocheretsa anthu a ku Israyeli ndi chisokonezo cha mtundu wa anthu kwambiri kotero kuti Mulungu anaganiza za kuthana nawo onse.
“Ndipo ndidzacotsa seta wako wonse: ndidzabweza oweruza ako monga poyamba, ndi aphungu ako monga paciyambi” Nsembe zimene sizimavomerezedwa ndi Mulungu zili monga, miyala yosakaniza, kusakaniza Choonadi cha Mulungu ndi zaumulungu onyenga za mtundu wa anthu.
Mulungu samavomereza nsembe zimene ndi zosakaniza. Zingaoneke zabwino m’maso mwa munthu, koma ngati ndi zosakaniza ndi zikhulupiliro zolakwika za mtundu wa anthu ndi zosakanizika ndi zosafunika ndipo motero ndizosavomerezedwa ndi Mulungu.
Mulungu anakalipira anthu a Israyeli, makamaka ampatuko, alaliki abodza ndi ochimwa.
Ngati tingawerenge Eksodo kapena Numeri, tingaone kuti Mulungu sanawakalipire onse poyamba. Mulungu anathandiza anthu a ku Israyeli ndi kukhuthura madalitso pa iwo. Koma Yoswa atafa, kuyambira pa Oweruza, anthu a ku Israyeli anali atalowerera.
Komabe, anasankha kuyenda m’njira zawo. Pa nthawi imeneyo, Mulungu anatuma m’neneri Yeremiya ndi kuuza Israyeli kuti azipereke ku Babulo.
Yeremiya anauza anthu kuti azipereke ku Babulo. Ichi chili ndi tanthauzo lauzimu, kusonyeza choona chakuti olungama amauza iwo amene akutsatira ampatuko kuti azipereke ku uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
MULUNGU AZUDZULA AMPATUKO
Kodi chifukwa chiyani Mulungu adzudzula ampatuko?
Chifukwa akutumikira mafano m’malo mwa Mulungu.
Kodi chifukwa n’chiyani atumiki a Mulungu anadzudzula anthu a Israyeli? Chifukwa chakuti anasintha ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe, anasankha anthu wamba kukhala ansembe, ndi kusintha masiku akuperekera nsembe.
Iwo anasintha Tsiku Lachitetezero cha machimo kuchoka pa tsiku lakhumi la mwezi wa chisanu ndi chiwiri kufika pa tsiku la khumi ndi chisanu la mwezi wa chisanu ndi chitatu ndi kusankha ansembe osakhala a Alevi. Motero anathetsa njira ya kubadwa mwatsopano.
Mulungu anadzudzula alaliki abodza. Iwo amene anatumikira ana ang’ombe agolide m’malo mwa Mulungu anakhala ansembe achinyengo.
Mwa choona, Mulungu sanadzudzule iwo chifukwa akulambira mafano kokha. Kodi inu ndi ine sitinalambirepo mafano nthawi ina? Timachimwa mobwereza, koma zolakwa zathu sizionedwa kukhala machimo akulu kokha chifukwa chakuti tili mu chisomo cha Mulungu. Koma kusinthanitsa Mulungu ndi ana ang’ombe agolide sikungakhululukidwe. Ndipo zimenezo zidzachitika chifukwa cha kusinthanitsa ndondomeko yoperekera nsembe ndi kusankha anthu wamba pa unsembe.
Kodi ndi uchimo oipa otani umenewu ulili! Ndi machimo akulu kwambiri. Kodi munthu angakhululukidwe bwanji atasinthanitsa Mulungu ndi ana ang’ombe agolide? Zinalembedwa M’baibulo kuti ndi unali uchimo wa Yerobiamu umene unabweretsa mkwiyo wa Mulungu.
Monga m’mene Mulungu anaonetsa mkwiyo Wake mu Chipangano Chakale, Iye tsopano akuononga ochimwa amene anaukira Iye. Mulungu anauza Israyeli kuti adzatembelera iwo amene sanabwerere mukulambira ana ang’ombe agolide.
AMPATUKO AMAPEREKA NSEMBE KUNJA KWA CHILAMULO
Kodi tiyenera kuchita chiyani tisanatumikire Mulungu?
Machimo athu onse atsukidwe
Mafumu ndi ansembe ampatuko a Israyeli anaukira Mulungu ndipo anasankha iwo amene sanalemekeze ndondomeko ya nsembe kwa unsembe. Yerobiamu, mfumu ndi malingaliro osokonekera, anaika wina amene sanali m’nyumba ya Levi kukha wansembe.
Okhawo amene anali m’nyumba ya Levi ndiwo ankayenera kukhala ansembe ndi kugwira ntchito mu chihema. Molondola kwambiri, ansembe ankayenera kukhala wa nyumba ya Aroni. Ili linali lamulo losatha la Mulungu. Koma Yerobiamu anaika ansembe akunja kwa nyumba ya Levi ndipo anawauza kupereka nsembe ku ana ang’ombe agolide. Tiyenera kudziwa m’mene ichi chinadzetsera ku mkwiyo wa Mulungu.
Ngakhale lero, iwo amene ndi osabadwa mwatsopano angakhale atumiki, akulu mpingo, ndi madikoni mu mpingo. Ichi chikuyenda moukira lamulo la Mulungu ndi kuitana mkwiyo Wake. Kodi Mulungu amasangalala ndi nsembe zosayeruzika? Ampatuko ayenera kuononga zosema zawo za golide ndi kubwerera kwa Mulungu ndi kubadwa mwatsopano.
Yesaya 1:10-17 inena kuti, “Invani mau a Yehova inu olamulira a Sodomu, cherani makutu ku cilamulo ca Mulungu wathu, inu anthu a Gomora. Nditani nazo nsembe zanu zocurukazo? Ati Yehova; ndakhuta nazo nsembe zopsereza za nkhosa zamphongo ndi mafuta a nyama zonenepa; sindisekera ndi mwazi wa ng’ombe zamphongo, ngakhale wa ana a nkhosa, ngakhale wa atonde. Pakudzaonekera inu pamaso pa Ine, ndani wafuna cimeneci m’dzanja lanu, kupondaponda m’mabwalo mwanga? Musadze nazonso, nsembe zacabecabe; nsembe zofukiza zindinyansa; tsiku lokhala mwezi ndi sabata, kumema masonkhano, sindingalole mphulupulu ndi masonkhano. Masiku anu okhala mwezi ndi nthawi za mapwando anu mtima wanga uzida; zindibvuta Ine; ndarema ndi kupirira nazo. Ndipo pamene mutambasula manja anu, ndidzakubisirani inu maso anga; inde pocurukitsa maphemphero anu Ine sindizamva; manja anu adzala mwazi. Sambani, dziyeretseni; cotsani maipidwe anu oipa pamaso panga; lekani kucita zoipa; phunzirani kucita zabwino; funani ciweruzo; thandizani osautsidwa, weruzirani ana amasiye, munenere akazi a masiye.’”
Ngati tingawerenge ndime imeneyi modekha, tingaone kuti atsogoleri azipembedzo a Israyeli anali odzipereka kwambiri. Koma zilibe kanthu kuti anali ozipereka motani, anaonongedwa chifukwa anapereka nsembe zolakwika ndipo anaphwanya lamulo la Mulungu.
Tingaone kuti iwo sanatsatire chilamulo cha Mulungu pamene ankapereka nsembe kapena kumvera mawu a Mulungu. Atsogoleri awa anali odzipereka kotero kuti anapanga zopereka zosawerengeka pamaso pa Mulungu. Baibulo linena kuti mwazi unkayenda ngati mtsinje mkati mwa chihema.
Komabe, Pamene Mulungu anaona zimene anachita, Iye anati uli ngati uchimo wa Gomola. Iye anaona kuti anali kupanga zopereka pamaso Pake, koma mwa choona, anali kuchimwa. Iye anati kunali kwabwino kuti asabweretse zopereka. Iye sanafune kuti azilandire.
Pamene anali kupereka nsembe pamaso pa ana ang’ombe agolide, Mulungu sanakhululukire machimo awo. Iye sanakwanitse kupilira nawo. Iye anawauza kuti anayenera kupereka nsembe mogwirizana ndi njira imene Iye analamula. Ngati sichoncho, kukanakhala bwino kwa iwo kusapereka nsembe konse.
Nsembe zawo sizinaperekedwe kwa Mulungu m’njira yabwino, ndipo chifukwa cha ichi, ansembe anali kuchimwa pamaso pa Mulungu. Muyenera kudziwa kuti kutumikira Mulungu ndi kuchita nchito Yake popanda kutsuka machimo anu ndi uchimo waukulu pamaso pa Iye.
AMPATUKO ALI NGATI APHUNZITSI A PA SUKULU
Kodi ampatuko amaphunzitsa chiyani?
Amaphunzitsa zamakhalidwe, osati m’mene angabadwire mwatsopano
Ampatuko kunja amaoneka oyera. Ngati atenga guwa, amaoneka ochita bwino kotero kuti ena amakopeka ndi kaonekedwe kawo. Amamveka anzeru kwambiri. Ndipo nthawi zonse mu mauthenga awo amachenjeza anthu kukhala abwino. Kodi ndi ulaliki otani umenewo? Kodi kusiyana ndi kotani pakati pa ulaliki wawo ndi maphunziro a aphunzitsi asukulu?
Mpingo wa Mulungu ndi malo amene obadwa mwatsopano amakhala pamodzi kuti alambire Mulungu. Mtundu wa mpingo otere okha ndiye mpingo oona. Mpingo oona wa Mulungu suyesa kuphunzitsa m’mene tiyenera kukhalira pamaso pa Mulungu. Olalika wa mpingo oona amalalikira za uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Zilibe kanthu kuti ndinu odwala motani, Mulungu anatsuka machimo anu onse.
Alaliki ampatuko amauza otsatira awo, “Chitani ichi, ndiponso chitani icho,” Kuika zolemetsa zambiri pa iwo, koma iwo okha sakufuna kunyamala chala kuti asunthe zolemetsazo.
Mlaliki wampatuko amagulira mwana wake fiyo odula ndi kutumiza mwana kukaphunzira ku maiko akunja. Kodi wansembe angakwanitse bwanji zimenezi? Kodi ndikuti kumene angatenge ndalama? Ngati angakhale ndi ndalama zotero, kodi sangagwiritsire nchito kulalikira uthenga wabwino? Kodi olalika ayenera kumayendetsa galimoto lokwera mtengo? Kodi ayenera kuyendetsa galimoto lapamwamba kuti akhale olemekezeka? Mlaliki amene akuyendetsa galimoto yokwera mtengo ndi wakuba. Pamene otsatira ake samatha kugula ngakhale galimoto lotsika mtengo, kodi kungakhale koyenera bwanji kwa iye kukhala ndi mtundu wa deluxe? Tingaone mlaliki wampatuko kokha mwa kuona zochita zake.
Alaliki ampatuko amapempha ndalama zambiri. Mipingo ina imalipira olalika awo ndalama zopitilira pa $10,000 pa mwezi. Ndipo iyi ndi yolipira ya boma yokha. Amawapatsa chindapusa cha zamaphunziro, chindapusa cha za mabuku, chindapusa cha kusamalira ana chindapusa choyendera kutchulako zotchepa chabe.
Ndipo ngakhale choncho, ena mwa iwo amadandaula kuti sakulipitidwa zokwanira. Amatenga $10,000 pa mwezi ndipo akupemphabe ndalama zambiri. Kodi $10,000 ndi malipiro ochepa otere? Olalika ayenera kukhutira ndi zimene apeza zokwanira pamene akupitiliza kuphunzitsa bwino uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Mlaliki oona amakonda kudzudzulidwa ndi mtendere wa kwa Mulungu. Koma mlaliki wampatuko amene alibe mtendere amafuna malipiro a ndalama. Alaliki otere mwa choona akulambira ana ang’ombe agolide.
Mpingo wa Mulungu nthawi zina umatchedwa Ziyoni. Palibe mpingo wina wokoma monga ziyoni. Mpingo wa Mulungu ndi malo amene uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ukulalikidwira.
Yesaya 1:21 anena kuti, “Mudzi wokhulupirika wasanduka wadama! Wodzala ciweruzowo! Cilungamo cinakhalamo koma tsopano ambanda.” Yesaya anatchula Mpingo wa Mulungu, kunena kuti, “Wodzala ciweruzowo”
Mulungu ndi wachilungamo komanso oongoka. Chifukwa ndife operewera, chifukwa ndife mbadwa za Adamu ndi kubadwira m’chimo, Yesu anabwera kudzikoli kudzatsuka machimo athu onse ndi madzi komanso Mzimu. Umu ndi m’mene Mulungu alili wapakatikati.
Mu Chipangano Chakale, pamene anthu ankadziwa kuti anali operewera, anali kubwera kwa Mulungu ndi kupereka nsembe. “Ndinachita cholakwika m’njira iyi ndi iyo. Ndinali olakwitsa. Ndiyeno anali kukhululukidwa machimo awo a masiku onse, ndiponso anali kutha kupeza chikhululukiro cha machimo awo a pa chaka kamodzi pa Tsiku Lachitetezero cha machimo.
Chimodzimodzi, mu Chipangano Chatsopano, Yesu anabwera kudzikoli ndipo anabatizidwa ndi kupachikidwa kuti atsuke machimo onse a mtundu wa anthu kamodzi kokha.
Koma pa msonkhano wa pa chaka chatsopano, anthu ambiri analira ndi kulapa, “Okondedwa Mulungu, chonde ndikhululukireni chifukwa cha machimo amene ndinachita chaka chatha. Ndipo chonde ndidalitseni mu chaka chatsopano.” Anthu amenewo ndi ampatuko,
Kodi ndiyeno, choonadi cha kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu ndi chiyani? Yesu anabwera kudzikoli pafupi fupi zaka zikwi ziwiri (2000) zapitazo, anatsuka machimo a mtundu wa anthu kamodzi kokha ndipo mwakutero anatipulumutsa ku uchimo kwamuyaya. Iye anatipulumutsa ku machimo onse a dziko ndi madzi komanso mwazi. Koma ngati tikupempha chikhululukiro cha masiku onse, Kodi Iye adzanena chiyani?
“Mudzi wokhulupirika wasanduka wadama! Wodzala ciweruzowo! Cilungamo cinakhalamo koma tsopano ambanda.” Aliyense amene akudzitcha kukhala ochimwa ndi wampatuko.
ANSEMBE AMPATUKO SANGALALIKIRE UTHENGA WABWINO WA KUBADWA MWATSOPANO MWA MADZI NDI MZIMU
Kodi Mulungu amamvera mapemphero a ochimwa?
Ai. Iye sangawamve chifukwa machimo awo anawapatula kwa Mulungu.
Ambuye wathu amaitana iwo amene akhulupilira mwa Iye ndi kuphempha chikhululukiro kuti ndi akupha. Popeza amapempha chikhululukiro ndiponso akunena kuti ndi ochimwa, kodi akuyembekezera kuti Yesu abwerenso kudzafera machimo awo kachiwiri? Ubatizo ndi Mtanda wa Yesu ndi zenizeni za chipulumutso.
Mu 1 Petro 3:21, akunena kuti ubatizo wa Yesu ndi chifaniziro cha chipulumutso chathu. Yesu Kristu anafa kamodzi kuti apulumutse mtundu wa anthu ku uchimo. Iye anatsuka machimo a mtundu wa anthu kamodzi kokha ndipo patatha masiku atatu anaukitsidwa. Iye tsopano wakhala kudzanja lamanja la Mulungu.
Yesu anabatizidwa kamodzi ndi kufa kamodzi pa mtanda kuti apulumutse ife ku machimo athu kwamuyaya. Iye anabatizidwa ndi yohane Mbatizi pamene anali ndi zaka makumi atatu (30). Iye anafa kamodzi kuti apulumutse ife ku machimo onse a dziko. Kodi izi sizikutanthauza kuti chiweruzo chinaperekedwa ku nthawi zonse?
Ngati ampatuko akunena kuti akali ochimwa, akupempha Iye kuti abwere kachiwiri ndi kupachikidwanso. Mwa choona, adzayenera kupitiliza kuchita choncho nthawi iliyonse pamene iwo akupempha chikhululukiro.
Iwo amene akukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu m’mitima yawo anapulumutsidwa ku uchimo kwamuyaya, akhala olungama, ndi kupita Kumwamba kukalandira madalitso a Mulungu ndi moyo osatha. Aliyense amene wakumana ndi chilungamo angapulumutsidwe kudzera mwa madzi ndi Mzimu ndi kukhala m’modzi wa anthu odalitsidwa wa Mulungu. Aliyense amene akupempha chilungamo cha chipulumutso pamaso pa Mulungu adzadalitsidwa.
Tiyeni tiwerenge Yesaya 1:18-20. “‘Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu ziri zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale ziri zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbu. Ngati inu muli ofuna ndi omvera, mudzadya zabwino za dziko, koma ngati mukana ndi kupanduka, mudzathedwa ndi lupanga; cifukwa mukamwa mwa Yehova mwatero. ”
Mulungu akutiuza kuti ngati ndife omvera ku uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, tidzadya zabwino za m’munda, koma ngati tikukana ndi kuukira, tizaonongedwa ndi lupanga.
Mulungu wathu anati, “Tiyeni tsopano, tiweruzane. Tiyeni tikambe. Kodi ndinu operewera? Kodi ndinu osalungama? Kodi mumazikonda nokha kwambiri? Kodi simungakhale mwa malamulo? Kodi simungachite zomwe lamulo likufuna? Mukudziwa koma simungakwanitse? Ndiyeno, bwerani kwa Ine. Ngakhale zoipa zanu ziri zofiira, zidzakhala oyera ngati matalala; ngakhale ziri zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wankhosa.” Ichi chikutanthauza kuti Mulungu anapulumutsa ochimwa molungama ndi kuwapanga kukhala achilungamo.
Panalibe uchimo pamene Mulungu analenga Adamu ndi Hava. Koma mwamsanga Satana anabwera kuzasokoneza. Iye anawayesa kuti asamvere Mulungu ndi kupanga mtundu onse wa anthu kukhala ochimwa mwa kuwapangitsa kuchimwa. Satana anapangitsa anthu kugwa. Pachiyambi, Adamu ndi Hava sanali ochimwa pamaso pa Mulungu. Anali kukhala ndi Mulungu m’munda wa Edeni. Koma anakhala ochimwa. Choncho tsopano, Mulungu akuitana ife. Tiyeni tsopano tiweruzane. Tiyeni tiweruzane!
“Kodi ndi machimo angati amene mwachita m’dzikoli? Ndipo ndi machimo angati omwe mudzachite musanafe?”
“Oho, Mulungu. Ndikosatheka kuti tisachimwe. Sitingakhale oyeretsedwa mulimonse m’mene tingayesere.”
“Chabwino, ndiyeno kodi ndi machimo angati amene mwachita kufikira tsopano?”
“Chabwino, Ambuye, sindingathe kukumbukira zonse, koma ochepa amene ali m’maganizo mwanga. Kodi mukukumbukira tsiku lija? Mukudziwa chimene ndikunena…ndiponso palinso nthawi ina ija, Mukudziwa…”
Ndiyeno Mulungu anati, “Choncho tiyeko pitiliza ndiuze Ine. Kodi uganiza kuti ndi zomwezo? Kodi ukudziwa ndi angati kuchotsako amenewo? Komabe, machimo onse amene ukukumbukira, machimo onse amene waiwalira, ndiponso ngakhale machimo onse amene udzachita mtsogolo, ndinawatsuko onse kwamuyaya. Koma osati ako okha, komanso a ana ako ndi ana a ana ako ndi machimo onse a mbadwa zako. Ndine Mulungu olungama. Ndinatsuka machimo ako onse kamodzi kokha.”
Mulungu, ndani anatsuka machimo a mtundu wa anthu kuchokera uchimo wa Adamu kufikira machimo onse a munthu womaliza padziko, ndi Alefa ndi Omega, Oyamba ndiponso Otsiriza,
“Ndine Mpulumutsi ndiponso Mulungu wamphamvu yonse.”
“Ine ndine Yehova, Mulungu wachifundo.”
“Ndizakhala ndi chifundo kwa iwo amene akuyenera chifundo, ndipo ndizakhala wachisoni kwa iwo akuyenera Chisoni.”
Ngati tingapemphe za chifundo Chake ndi kukhala omasuka ndi Iye, tingakhale ndi chifundo cha Mulungu. Atate wathu akufuna kudalitsa ife tonse. Iye akufuna ife tonse tikhale olungama. Mu chikondi Chake ndi chifundo, Iye akufuna kupanga ife tonse kukhala ana Ake olungama.
Kodi Mulungu akufuna kuti ife tichite chiyani pamene tabadwa mwatsopano?
Akufuna ife tilalikire uthenga wabwino padziko lonse lapansi.
Iye akufuna kuti ife tikhale oyera ngati matalala. Yesu anatsuka machimo a mtundu wa anthu kamodzi kokha kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi Wake. Ngati mpingo ukulephera kuthana ndi mavuto a uchimo ndi moyo wa okhulupilira ake onse, sungatchulidwe kuti mpingo oona wa Mulungu.
Anthu amabwera kwa ansembe ndi kuwafunsa, “Ndili ndi uchimo. Kodi ndichite chiyani? Ndimalapa ndipo ndalapa kwa nthawi yaitali kwambiri, koma machimo anga sakuchoka. Sindingathe kupitiliza kukhala nawonso. Sindiganiza kuti tingapitilize kukhala ndi moyo wanga wa chipembedzo.” Ngati wansembe sangapereke yankho lolondola ku mavuto ake, ndiye kuti ndi wampatuko. Iye mwina anganene kuti, Ndi kufuna kwako. Pita kapemphere ku phiri. Yesa kusala chakudya kwa masiku- makumi anayi (40).”
Ansembe ampatuko kapena atsogoleri azipembezo ali odzala ndi zodetsedwa kotero kuti sadziwa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Sakudziwa kuti mwina miyoyo yawo idzapita ku gehena kapena Kumwamba.
Atsogoleri amenewo sakuchita bwino pamaso pa Mulungu. Iwo ndi Akristu abodza ndi ampatuko. Akuoneka ngati amakhulupilira mwa Yesu kunja kwake, koma mitima yawo ndi yodzalabe ndi uchimo. Iwo sanatsukidwe ku machimo awo. Iwo sangathe kulalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu umene ungatsuke machimo awo onse. Tiyeni tisanyengedwe ndi iwo.
Tito 3:10-11 akunena za ampatuko, “Munthu wopatukira cikhulupiriro, utamcenjeza kamodzi ndi kawiri, umkanize, podziwa kuti wotereyo wasandukira konse, nacimwa, nakhala wodzitsutsa yekha.” Chifukwa akukhulupilira mwa Yesu koma nsi osabadwa mwatsopano, amadzitsutsa okha kuti ndi ochimwa. Iwo amanyalanyaza ndi kuponda pa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, ndi kunena kuti ndi ochimwa amene sangathe koma kupita ku gehena.
Iwo ndi ampatuko mu Chikristu. Aliyense amene akhulupilira mwa Yesu ndipo ali ndi uchimo ndi wampatuko. Ampatuko amasiyana ndi Mulungu. Mulungu ndi oyera. Koma iwo ndi osayera. Iwo amene akhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndi oyeretsedwa ku machimo awo onse. Motero, aliyense amene akhulupilira mwa Yesu ndipo ali ndi uchimo ndi wampatuko. Tiyenera kukhala kutali ndi iwo amene akunena kuti akukhulupilira mwa Mulungu koma akali ochimwa.
Tiyeni tilalikire uthenga wabwino kwa iwo amene sanamvepo ndi iwo amene akufuna kukhala okhulupilira koma sangathe chifukwa sakuudziwa. Tiyeni tiwathandize kuti akhale obadwa mwatsopano. Tiyeni tilimbane nawo iwo amene akuima m’njira ya uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Tiyenera kulalikira uthenga wa kubadwa mwatsopano wa madzi ndi Mzimu padziko lonse lapansi. Ame!