(Ekisodo 12:43-49)“Ndipo Yehova anati kwa Mose ndi Aroni, lembani la Paskha ndi ili: mwana wa mlembo ali yense asadyeko; koma kapolo wa mwini ali yense, wogula ndi ndarama, utamdula, ndipo adyeko. Mlembo kapena wolembedwa nchito asadyeko. Audye m’nyumba imodzi; usaturukira nayo kubwalo nyama yina; ndipo musathyole pfupa lace. Msonkhano wonse wa Israyeli uzicita ici. Koma akhale nanu mlendo, nakonzera Yehova Paskha, adulidwe amuna ace onse, ndipo pamenepo asendere kuucita; nakhale ngati wobadwa m’dziko; koma wosadulidwa ali yense asadyeko. Pakhale lamulo lomweli pa wobadwa m’dziko, ndi pa mlendo wakukhala pakati pa inu.”
Kodi lamulo lofunikira kwambiri ku Aisrayeli kuti akhale ana a Mulungu mu Chipangano cha Kale linali lotani?
Iwo anali kuyenera kudulidwa.
Mawu a Mulungu monse mu Chipangano cha kale ndi Chatsopano ndi ofunikira ndiponso apamwamba ku onse aife amene takukhulupilira mwa Mulungu. Sitingakhale osasamala ngakhale liwu limodzi la mawuwo chifukwa mawu a Mulungu ndi mawu a moyo.
Ndime ya tsiku lalero ikutiudza kuti wina aliyense amene akufuna kusunga Paskha ayenera kudulidwa nthawi isanakwane. Tiyenera kuganiza chifukwa chimene Mulungu akutiuza zimenezi. Ngati munthu sanadulidwe, sangasunge Paskha.
Ngati tikufuna kukhulupilira mwa Yesu, tiyenera kumvetsetsa cholinga cha Mulungu pakutipatsa lamuloli. Mdulidwe ndi kudula kwa khungu lawo lakusonga. Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu anauza Abrahamu ndi a m’banja lake kuti azidulidwa? Cifukwa ndi chakuti Iye analonjeza kuti okhawo amene “adula” machimo awo angakhale anthu Ake.
Ichi n’chifukwa Iye akuuza anthu a Israyeli mu Chipangano cha Kale kuti adulidwe. Kuti akhale anthu a Mulungu, anthu a Israyeli anayenera kudulidwa. Linali lamulo Lake, kuimilira pakuyeretsa, ndipo Iye anakhala Mulungu wa omwe adamasulidwa kumachimo awo mwa chikhulupiliro kupitira mu mdulidwe. Moonjezera, mu Chipangano cha Tsopano, Iye amakhala Mulungu wa aja amene adula uchimo mwa chikhulupiliro.
PASKHA
Kodi Paskha chinali chiyani?
Linali tsiku la Aisrayeli lokumbukila ndi kuthokoza Mulungu chifukwa cha Eksodo kuchoka ku Igupto.
Tchuthi chofunikira kwambiri cha anthu a Aisrayeli chinali Paskha. Linali tsiku lokumbukira ndi kuthokoza Mulungu chifukwa cha Eksodo kuchoka ku Igupto, kumene Aisrayeli anakhala akapolo kwa zaka pafupifupi zokwanira mazana anayi (400). Mulungu anagwetsa miliri yokwanira khumi kuti asinthe mtima ouma wa Farao. Inali njira yotereyi imene Iye anatulutsira anthu a Israyeli mu Iguputo ndi kuwatengera kudziko la Kanani.
Anthu a Israyeli anapulumutsidwa ku imfa ya ana oyamba kubadwa, muliri otsiriza, kudzera mu mwana wa nkhosa operekedwa nsembe ndi mdulidwe. Choncho, Mulungu anawauza kuti asunge Paskha mu m’badwo wawo wonse ngati chikumbutso cha chifundo Chake.
KODI AISRAYELI AYENERA KUCHITA CHIYANI KUTI ASUNGE PASKHA?
Kodi Aisrayeli anayenera kuchita chiyani kuti asunge Paskha?
Anayenera kudulidwa.
Tiyenera kumvetsetsa kuti pofuna kusunga Paskha mu uzimu, tiyenera kudulidwa m`mitima yathu. Ngakhalenso anthu a Israyeli anayenera kudulidwa kuti alemekeze Paskha.
Kunalembedwa mu Eksodo 12:43-49. “Ndipo anati kwa Mose ndi Aroni, lembani la Paskha ndi ili: mwana wa mlembo ali yense asadyeko; koma kapolo wa mwini ali yense, wogula ndi ndarama, utamdula, ndipo adyeko. Mlembo kapena wolembedwa nchito asadyeko. Audye m’nyumba imodzi; usaturukira nayo kubwalo nyama yina; ndipo musathyole pfupa lace. Msonkhano wonse wa Israyeli uzicita ici. Koma akhale nanu mlendo, nakonzera Yehova Paskha, adulidwe amuna ace onse, ndipo pamenepo asendere kuucita; nakhale ngati wobadwa m’dziko; koma wosadulidwa ali yense asadyeko. Pakhale lamulo lomweli pa wobadwa m’dziko, ndi pa mlendo wakukhala pakati pa inu.” Motero anauza Aisrayeli kuti asunge Paskha atadulidwa.
Kodi ndi ndani amene anali kuloledwa kudya nyama ya mwana wa nkhosa wa Paskha ndi kusunga Paskha? Okhawo amene anali odulidwa ndiwo anali kusunga Paskha.
Mwana wa nkhosa wa Paskha, monga m`mene tonse tikudziwira, ndi Yesu Kristu amene anachotsa machimo onse adziko.
Ndiyeno, kodi mdulidwe n’chiyani mu Chipangano cha Kale ndi mu Chipangano cha Tsopano? Mdulidwe ukutanthauza kudula kwa khungu lakunsonga. Yesu Kristu nayenso anadulidwa masiku asanu ndi atatu atabadwa padzikoli. Mulungu analamula kuti wina aliyense amene akutengako mbali mu mwambo wa Paskha ayenera kudulidwa, ndipo ankaonetsetsa kuti wina aliyense amene sanadulidwe asatengeko mbali mu Paskha.
Motero, wina aliyense ayenera kudulidwa monga m`mene Mulungu anakonzera. Ngati mkukhulupilira mwa Yesu, muyenera kumvetsetsa tanthauza la mdulidwe mu Chipangano Chatsopano.
KODI MWAMBO WA MDULIDWE UMENE MULUNGU ANALAMULO ABRAHAMU KUCHITA UNALI OTANI?
Kodi Abrahamu ndi a m’banja lake anali kukhala ana a mulungu motani?
Mwa kudulidwa
Mu Genesis, Mulungu anaonekera kwa Abrahamu ndipo anapanga pangano Lake ndi iye ndiponso ndi a m’banja lake. Mu ndime ya 15, Mulungu analonjeza kuti am’banja la Abrahamu adzachuluka ngati nyenyezi mu mitambo ndi kuti Iye adzawapatsa dziko la Kanani ngati cholowa chawo.
Ndipo mu ndime ya 17, Iye anauza Abrahamu kuti ngati iye ndi am’banja lake analowa mu pangano Lake ndi kudulidwa, Iye adzakhala Mulungu wawo ndipo iwo adzakhala anthu Ake. Linali pangano la Mulungu kwa Abrahamu ndi am’banja lake. Mulungu analonjeza kuti ngati anakhulupilira pangano Lake ndipo anadulidwa, chingatanthauze kuti akhala anthu Ake, ndipo Iye adzakhaladi Mulungu wawo.
Genesis 17:7-8 akuti, “Ndipo ndidzalimbitsa pangano langa ndi Ine ndi iwe pa mbeu zako za pambuyo pako m’mibadwo yao, kuti likhale pangano la nthawi zonse, kuti ndikhale Mulungu wako ndi wa mbeu zako za pambuyo pako. Ndipo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako, dziko la maulendo anu, dziko lonse la kanani likhale lako nthawi zonse: ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao.”
Mdulidwe unali chizindikiro cha pangano la Mulungu pakati pa Abrahamu ndi am’banja lake.
KODI MDULIDWE WA UZIMU UKUTANTHAUZA CHIYANI?
Kodi mdulidwe wa uzimu ndi chiyani?
Ndi kudula machimo onse a m`mitima yathu pokhulupilira mu ubatizo wa Yesu.
Chifukwa Abrahamu anakhulupilira mu mawu a Mulungu, Mulungu anamupanga iye kukhala olungama ndipo anamupanga kukhala mwana Wake. Unali mdulidwe umene unali chizindikiro cha pangano pakati pa Mulungu ndi Abrahamu.
“Ili ndi pangano limene uzisunga pakati pa Ine ndi iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako: azidulidwa amuna onse a mwa inu.” (Genesis 17:10).
Mdulidwe wa kuthupi ukutanthauza kudula kwa khungu lakusonga: mu uzimu, ukutanthauzanso kupereka machimo athu onse pa Yesu kupitira mu chikhulupiliro chathu mu ubatizo Wake. Ndife odulidwa mu uzimu pamene tadula machimo athu onse pakubvomera chipulumutso cha ubatizo wa Yesu. Mdulidwe m’Chipangano Chatsopano ndi kudula machimo athu onse kudzera mu ubatizo wa Yesu.
Choncho mdulidwe mu Chipangano cha Kale ndi ubatizo wa Yesu mu Chipangano Chatsopano, ndipo onse ndi mapangano a Mulungu, amene akutipanga kukhala anthu Ake. Motero mdulidwe mu Chipangano cha Kale komanso ubatizo wa Yesu mu Chipangano Chatsopano ndi chinthu chimodzi ndipo chofanana.
Monga m`mene a m’banja la Abrahamu anakhala anthu a Mulungu pamene anadula khungu lawo lakusonga, takhala ana a Mulungu pamene tadula machimo onse mu mtima mwathu. Tikuchita ichi mwa kukhulupilira kuti mulibe uchimo mdziko chifukwa Yesu anachotsa machimo onse pamene Iye anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi.
Ubatizo wa Yesu amapanga ochimwa onse kukhala wolungama mwakudula machimo awo. Monga m`mene chiduswa cha khungu chinali kuchotsedwa mwanjira ya mdulidwe, momwemo machimo a anthu anadulidwa m’mitima yonse ya anthu pamene Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi pa Yordano. Onse amene akukhulupilira izi angadulidwe mu uzimu ndi kukhala anthu a Mulungu, wolungama.
CHIKHULUPILIRO CHABODZA CHIMENE CHIKUPANGITSA ANTHU KUDZIDULA IWO OKHA KWA MULUNGU
Kodi n’chiyani chinapanga Aisrayeli kudzilekanitsa iwo okha kwa Mulungu?
Kusadulidwa
Mulungu anaudza Abrahamu kuti munthu aliyense osadulidwa ayenera kuchotsedwa ku anthu Ake. Ndiyeno, kodi mdulidwe n’chiyani? Ndipo kodi mdulidwe wa uzimu n’chiyani? Ngati mdulidwe wa kuthupi ndi kudula chikopa pang’ono kuchoka kuchigawo cha thupi, ndiye kuti mdulidwe wa uzimu ndi kudula uchimo wonse m’mitima yathu ndi kuupereka pa Yesu kudzera mu ubatizo Wake.
Ubatizo wa Yesu ndi mdulidwe wa uzimu wa anthu, umene unadula machimo onse adziko kwaife ndi kuperekedwa pa Yesu. Chifukwa cimene Yesu anabatizidwira ndi Yohane Mbatizi chinali kupulumutsa anthu onse kudzera mu mdulidwe wa uzimu, umene kunachotsa uchimo onse.
Machimo onse a anthu anaperekedwa pa Yesu. Mulungu, wokhala Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, Mulungu wa Yakobo, ndi Mulungu wa mibadwo yawo yonse, anapanga pangano ndi Abrahamu ndi mibadwo yake yonse ndipo anawadula khungu lawo lakunsonga. Ndi m`mene Iye anakhalira Mulungu, M’pulumutsi wa onse amene anadula machimo awo kudzera mu mdulidwe.
Kodi mdulidwe umene ukudula uchimo ndi chiani? Ndi pangano la Mulungu ndi Abrahamu ndi onse aja amene anabadwa mwatsopano pokhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi imfa Yake pa Mtanda ngati chipulumutso chawo. Mwanjira imeneyi, Iye anatipatsa ufulu okhala anthu ake. Motero Iye ndi Mulungu wa aja amene anadulidwa.
Mulungu ananena kwa Abrahamu. “A masiku asanu ndi atatu azidulidwa mwa inu, ana amuna onse a m’mibadwo mwanu, amene abadwa m’nyumba ndi amene agulidwa ndi ndalama kwa alendo ali onse, wosakhala mwa mbeu zako Azidulidwatu amene abadwa m’nyumba mwako ndi amene agulidwa ndi ndalama zako: ndipo pangano langa lidzakhala m’thupi mwako pangano losatha. Ndipo mwamuna wosadulidwa khungu lace, munthuyo amsadze mwa athu a mtundu wace; waphwanya pangano langa…” (Genesis 17:12-14).
Aliyense amene afuna kubwera kwa Yesu popanda mdulidwe wa uzimu azadulidwa ku anthu Ake. Mdulidwe wa uzimu ndi ubatizo wa Yesu mu Chipangano Chatsopano, umeneo machimo onse adziko anaperekedwa pa Iye.
Wina aliyense amene akhulupilira mwa Yesu ayenera kukhulupiliranso mu mdulidwe wa m’Chipangano cha Kale ndi ubatizo wa Yesu mu Chipangano Chatsopano, kuti alandire Mzimu, apulumutsidwe kumachimo onse, ndikukhala mwana wa Mulungu. Kwa ife amene tikukhulupilira mwa Yesu, mdulidwe wa Chipangano Chakale ndi ubatizo wa Yesu mu Chipangano Chatsopano ndi chimodzimodzi.
Ngati tilephera kudziwa tanthauzo leni-leni la mdulidwe kapena sitingabvomele m’mitima yathu chipulumutso kudzera mu mdulidwe wa uzimu umene umatilora kuti tibadwe mwatsopano, chikhulupiliro chathu chidzakhala pa chabe. Tingaganize kuti ndife okhulupililika kwa Mulungu, koma ziri ngati tamanga nyumba yathu yachikhulupiliro pa mchenga.
Mulungu akuuza onse aja amene akumukhulupilira mwa Iye kuti adulidwe, kukhulupilira mu chiombolo kudzera mu ubatizo wa Yesu, mdulidwe wa uzimu. Popanda mdulidwe, sitingakhale anthu Ake. Popanda mdulidwe, tiyenera kuchotsedwa mgulu la anthu Ake. Motero Mulungu analamula kuti aliyense, kaya anagulidwa ndi ndalama kapena anali mlendo, ayenera kudulidwa asanatengeko mbali mu chikondwelero cha Paskha.
Ngakhale nzika za Israyeli zinali kudulidwa ku anthu Ake ngati sanadulidwe. Pangano la Mulungu ndi anthu a Israyeli liyeneranso kugwiritsidwa ntchito ku onse amene akukhulupilira mwa Yesu.
Mu Eksodo 12, Anthu a Israyeli amene anali kudya nyama ya Paskha ndi masamba owawasa anayenera kukhala odulidwa kale. Ufulu wakudwa nyama ya Paskha unali kuperekedwa kwa okhawo amene anadulidwa.
N’chofunikira kwa ife kudziwa kuti pamene anthu Israyeli anadya nyama ya Paskha ndi kuika mwazi wa mwana wa nkhosa pa mwamba pazitseko za nyumba zawo, iwo anali odulidwa kale.
Mwa chilamulo cha Mulungu, ngati munthu sanadulidwe, iye ayenera kuchotsedwa ku anthu Ake ndi kutaya ufulu okhala m’modzi wa ana a Mulungu. Izi zikutanthauza kuti uchimo wa kusakhulupilira mu mdulidwe wa uzimu ukutengera anthu kuchionongeko. Okhawo amene anadulidwa mu uzimu kudzera mu ubatizo wa Yesu angapulumutsidwe.
“Cimenenso cifaniziro cace cikupulumutsani tsopano, ndico ubatizo,” (1 Petro 3:21). Kodi mukukhulupiliradi kuti machimo anu onse anaperekedwa pa Yesu kudzera mu ubatizo Wake mu Yordano? Ngati mukumvetsetsadi ndi kukhulupilira choonadi, ubatizo wa Yesu ndi mwazi ake, mudzazindikira kuti munadulidwa mu uzimu ndipo ndinu wolungama. Ndipo mudzakhalanso ndi chikhulupiliro mchoonadi cha uzimu kuti mwazi a Yesu pa Mtanda ukanakhala opanda ntchito popanda ubatizo Wake.
Kukanakhala kuti mukukhulupilira pa Mtanda wa Yesu popanda kudulidwa mu uzimu kudzera mu chikhulupiliro cha ubatizo wa Yesu, mukanazipeza nokha ochotsedwa kuchifundo cha Mulungu. Mukanazipeza kuti muli ndi uchimo m’mtima mwanu.
Tiyenera kukhulupilira mu choona chakuti chiombolo cha Mulungu chinayamba ndi ubatizo wa Yesu Kristu ndipo chinakwanilitsidwa ndi mwazi wake pa Mtanda. Kuti tichite chonchi, tiyenera kusunga m’mitima yathu mawu achoona, ubatizo wa Yesu ndi mwazi ake, ngati chipulumutso chathu.
Ndi chikhulupiliro ichi, tingaomboledwe ku mphamvu yamdima ndi kukhala ana akuunika. Chikhulupilirochi mu uzimu chikupatula aja amene anabadwadi mwatsopano kuchoka kugulu la okhulupilira wamba.
Ambuye wathu, Yesu, akutiuza kuti tikhale mwa Iye. Iye anachotsa kale machimo adziko kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi ake. Choncho, kuti tikhale ndi chizindikiro cha kukhala anthu a Mulungu, tiyenera kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu. Ngati tikulephera kuchita chonchi, tidzachotsedwa kwa Iye.
Chipulumutso choomboledwa ndi chosaposa ubatizo wa Yesu mu Chipangano Chatsopano ndi mdulidwe mu Chipangano ChaKale. Chipulumutso chimakwaniritsidwa ngati tili ndi chikhulupiliro mu ubatizo wa Yesu (mdulidwe wa uzimu) ndi mwazi Wake pa Mtanda ( mwazi wa mwana wa Nkhosa wa Paskha).
Mdulidwe wa kuthupi mu Chipangano Chakale ukulumikizana ndi ubatizo wa Yesu Kristu mu Chipagano Chatsopano. Yesaya 34:16 amatiuza kuti mawu alionse mu Baibulo ali ndi ogwirizana nawo. “Funani inu m’buku la Yehova, nimuwerenge; kulibe umodzi wa iye udzasowa, palibe umodzi udzasowa unzace; pakuti pakamwa pa Yehova panena, ndipo Mzimu wace wasonkhanitsa iwo.”
Liwu lililonse mu Chipangano Chakale likulumikizana ndi lina mu Chipangano Chatsopano. Kulibe liwu ngakhale limodzi la Mulungu likusoweka linzake.
KODI NANGA AJA AMENE AKHULUPILIRA MOPUSA MWA MKHALIDWE OSAYENERA?
Kodi n’ndani amene adzapita kugahena pakati pa okhulupilira onse mdziko?
Onse aja amene sakhulupilira mu mdulidwe Wa uzimu
Masiku ano kuli ambiri amene amakhulupilira mu mwazi okha wa Mwana wa nkhosa wa Paskha. Amafunsa, “Kodi mukutanthauza chiyani, mdulidwe? Unagwiritsidwa ntchito ku Ayunda okha m’nthawi ya Chipangano Chakale. Sitiyenera kudula khungu lathu lakunsonga m’nthawi ya Chipangano Chatsopano.”
Indedi n’zoona. Sikundinena kuti tiyenera kudulidwa kuthupi. Mtumwi Paulo anafotokoza mdulidwe wa uzimu momveka bwino, ndipo ndi mdulidwe wa mumtima umene Ndikunena tsopano.
Sindikuuzani kuti mudulidwe kuthupi. Mdulidwe wa kuthupi siutanthauza kanthu kwaife, koma tiyenera kubwera kwa Yesu kuti tidulidwe ku uzimu mwa kukhulupilira mu ubadizo wa Yesu kuti tipulumutsidwe kumachimo athu onse.
Kuti munthu abadwe mwatsopano, ayenera kudulidwa mu uzimu. Munthu aliyense wokhulupilira mwa Yesu ayenera kudulidwa mu uzimu. Ndinjira yokhayo yodulira machimo athu onse, njira yokhayo yoti tikhale olungama. Pokhapo utachitika mdulidwe wathu wa uzimu ndi pamene tingakhale wopanda uchimo mwathunthu. Choncho tiyenera kubvomera m’mitima yathu mdulidwe wa mu uzimu mwa kukhulupilira mu ubadizo wa Yesu.
Mtumwi Paulo nayenso anakhulupilira mu kufunika kwa mdulidwe wa mu uzimu. Iye anati, “ndipo mdulidwe uli wa mtima” (Aroma 2:29). Wina aliyense waife ayenera kudulidwa mu mzimu kuti amasulidwe ku uchimo.
Kodi machimo anu anaperekedwa kwa Yesu pamene anadulidwa kwa inu? Ngakhalenso mu Chipangano Chatsopano, iwo amene amakhulupilira mwa Yesu ayenera kudulidwa m’mitima yawo mwa kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu.
Mtumwi Paulo ananena ichi momveka bwino mu Makalata ake. Mulungu anapulumutsa anthu onse kumachimo adziko, anawapanga kukhala anthu Ake. Anthu a Israyeli anakhala anthu Ake mwa kuchotsa khungu lawo lakunsonga ndipo ife tikukhala ana Ake ngati tapereka machimo athu pa Yesu mwa kukhulupilira mu ubatizo Wake.
Mulungu amatilandira ngati ana Ake ngati Iye akuona chikhulupiliro chathu mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda. Chikhulupiliro ichi chikutipangitsa kuti tidulidwe mu uzimu ndipo chikutitengera kuchipulumutso chathu.
CHIPULUMUTSO CHIKUPEZEKA CHIFUKWA CHA OCHIMWA KUDZERA MU UBATIZO WA YESU NDI MWAZI WAKE
Kodi chipulumutso Chinakwaniritsidwa motani ndi Yesu?
Kupitira mu ubatizo Wake ndi imfa Yake pa Mtanda
Chipulumutso chimene Yesu anakwaniritsa kudzera mu madzi a ubatizo Wake ndi mwazi Wake pamtanda ndi cha ochimwa. Mwazi wa Mwana wa nkhosa unali chiweruzo, ndipo ubatizo wa Yesu unali mdulidwe wa uzimu umene unapereka machimo athu onse pa Yesu.
Mipingo ya Chikristu masiku ano sikufunika kupeputsa za chikhulupiliro ichi cha mdulidwe wa mzimu. Ngakhale kuti mdulidwe wa mu Chipangano Chakale ukutanthauza zochepa kwa ife masiku ano, ubatizo wa Yesu suyenera kutaidwa.
Ndinakuuzani kuti machimo anu anachotsedwa mwa ubatizo wa Yesu, ndipo ubatizo wa Yesu unakupulumutsani kumachimo anu onse. Kodi mu kukhulupilira mu izi? Ngati munyalanyaza ubatizo wa Yesu, simudzadziwa uthenga wabwino wa kubadwa mwatsopano, uthenga wabwino wa chiombolo chathunthu kudzera mu ubatizo wa Yesu.
Kodi tinganyaranyaze bwanji ubatizo wa Yesu, mdulidwe wa uzimu umene Mulungu amatiuza? Ngati tawerenga Baibulo, tikhonza kuona kuti mdulidwe ndi mwazi wa Mwana wa nkhosa wa Paskha ndi zogwirizana. Ichi ndi chisinsi cha mdulidwe wa uzimu, ubatizo wa Yesu.
Uthenga wabwino omwe ankalalikira Mtumwi Yohane unali wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi ake pa Mtanda. Iye anati mu 1 Yohane 5:6, “Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, ndiye Yesu Kristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi.”
Iye anati Yesu anabwera mwa madzi, mwazi ndi Mzimu. Osati mwa madzi okha, ndipo osati mwa mwazi okha, koma mwa madzi, mwazi ndi Mzimu zonse pamodzi. Zinthu zitatuzi, ubatizo wa Yesu, mwazi wa Yesu pa Mtanda ndi kuuka Kwake kwa akufa, ndi chimodzi, chitsimikizo cha chipulumutso chathu.
KODI N’CHIFUKWA CHIYANI BAIBULO IKULANKHULA ZA UBATIZO WA YESU NDI MWAZI AKE?
Kodi anthu a Israyeli anapulumutsidwa kudzera mu mwazi okha wa mwana wa nkhosa pa Paskha?
Ai. Iwo anali atadulidwa kale asanasunge Paskha.
Ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake ndi umene amatilora kuti tibadwe mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Eksodo 12 ikuti, “Zitengeleni mwana wa nkhosa, ndipo tengani mwazi wake mupake pa mphuthu za m’mbali azitseko ndi mphuthu za pamwamba m’nyumba zanu. Ndikaona mwazi, Ndizakupitilirani.”
Mukudziwa ichi, kodi n’kotheka kuti tingapulumutsidwe kumachimo athu onse mwa kukhulupilira mu mwazi okha wa mwana wa nkhosa wa Paskha? Kodi chifukwa n’chiyani ubatizo wa Yesu ukunenedwa kwambiri mu Chipangano Chatsopano? Atumwi anati, “popeza munaikidwa m’manda pamodzi ndi Iye muubatizo” (Akolose 2:12). “Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Kristu mudabvala Kristu” (Agalatiya 3:27). “...Cimenenso cifaniziro cace cikupulumutsani tsopano, ndico ubatizo” (1 Petulo 3:21).
Atumwi, Petro ndi Paulo ndiponso ophunzira ena onse a Yesu Kristu analalankhula za ubatizo wa Yesu. Ndi ubatizo wa Yesu mu Yordano umene anali kunena, ndipo ndi chikhulupiliro mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda umene ndi choonadi cha kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.
Kukuuzani choonadi, Ndinkakhulupilira mwa Yesu, koma mu mwazi Wake okha, kopitilira zaka khumi, popanda kuzindikira ngakhalenso ubatizo wa Yesu. Koma kuzindikira pa mwazi okha sikunachotse machimo m’mutima mwanga. Ndinakhulupilira mwa Yesu ndi mtima wanga wonse, koma mtima wanga unali wodzazabe ndi uchimo.
Patapita zaka khumi, Ndinazindikira tanthauzo la kudulidwa kwa mu uzimu (ubatizo wa Yesu) ndipo kenako Ndinabadwa mwatsopano. Pamenepo ndi pamene Ndinazindikira choonadi: Mdulidwe mu Chipangano Chakale ukuimilira ubatizo wa Yesu mu Chipangano Chatsopano. Ndinakhulupilira mu chimenecho ndipo Ndikukhulupilirabe.
“Mu Chipangano Chatsopano, kodi ndi chikhulupiliro choyenera kukhulupilira zonse mwazi wa Yesu ndi ubatizo Wake? Kodi chikhulupiliro changa n’choyenra mogwirizana ndi Baibulo?” Nditabadwa mwatsopano, Ndinadabwa ndi zinthuzi zimenezi.
Ngakhale kuti Ndinakhulupilira mu uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, mafunso anakhalabe m’mtima wanga. “Kodi n’choyenera kukhulupilira choonadi chakuti machimo anga onse anaperekedwa kwa Yesu pamene Iye anabadizidwa kapena n’choyenera kukhulupilira kuti Yesu anatipulumutsa kudzera mu imfa Yake yokha pa Mtanda? Kodi n’chokwanira kukhulupilira kuti Yesu ndi Mulungu ndi Mpulumutsi wanga kokha?” Ndinaganizira paizi pamene ndinkawerenga mu Eksodo 12.
Anthu ambiri masiku ano akuwerenga Eksodo 12 ndipo mosaganizira kawiri za kunena kuti Yesu Kristu anafa pa Mtanda ngati Mpulumutsi wawo. Amaganiza kuti n’koyenera kukhulupilira mu magazi a Kristu ndipo amapereka umboni wa choonadi cha chitsimikizo chawo. Angakhalupilire molimbika ndi kunena kuti Ambuye ndi Kristu ndiponso Mwana wa Mulungu komabe akali ochimwabe. Amaganiza kuti akakhulupilira kuti Yesu Kristu ndi Mpulumutsi wawo, adzapulumutsidwa angakhale kuti ali uchimo m’mitima yawo.
Mtundu wa chikhulupiliro ichi sioona. Chikhulupiliro chokhachi sichingawathandize kuti abadwenso mwatsopano. Ubatizo wa Yesu okha ndi mwazi Wake amatipangitsa ife kukhala wolungama.
Ndiyeno, kodi Eksodo 12 akutanthauza kweni-kweni chiyani? Ndinasanthula mu Baibulo, kuganiza, “Kodi pali bvuto lililonse la kukhulupilira mu mwazi wokha wa Yesu ndi kunyaranyaza ubatizo Wake?” Ngakhalenso Ndisanatsirize kuwerenga Ekisodo, Ndinazindikira choonadi kuti chipulumutso si cha mwazi okha wa Kristu koma ndi ubatizonso Wake. Kudzera mu Baibulo, Ndinatsimikizika kuti tidulidwa m’mitima yathu kudzera mu ubatizo wa Yesu chimodzi-modzinso ndi mu mwazi Wake pa Mtanda.
Kodi chifukwa n’chiyani Akristu Ambiri akadali ochimwabe?
Chifukwa sakukhulupilira mu ubatizo wa Yesu.
Ndinazindikira mu Ekisodo 12:47-49 kuti munthu asanaloledwe kudya nyama ya Paskha, anayenera kuti adulidwe. Ndi chifukwa chimenechi Mulungu akunena mndime ya 49, “Pakhale lamulo lomweli pa wobadwa m’dziko, ndi pa mlendo wakukhala pakuti pa inu.”
Pachifukwa ichi, aliyense amene sanali odulidwa sanali kudya nyama ya Paskha. Ichi ndi choonadi chimene Ndinapeza. Chimodzi-modzinso, pamene takhulupilira mwa Yesu ngati Mphulumusi wathu, poyamba tiyenera kuvomera choonadi chakuti machimo athu onse anaperekedwa pa Yesu kudzera mu ubatizo Wake mu Yordano ndipo kenako kuvomereza choona chakuti Yesu Kristu anafa pa Mtanda chifukwa cha machimowa.
Pamene Ndinadzindikira kuti Yesu anafa pa Mtanda kuti aweruzidwe chifukwa cha machimo anatenga kupitira mu ubadizo Wake, Ndinadzindikiranso tanthauzo la mdulidwe wa uzimu umene unatipulumutsa kumachimo athu onse ndi kuzolakwa za m’dziko.
Panthawiyo, Ndinadzindikira kuti machimo anga onse anatha. Mtima wanga unayera ngati matalala ndipo potsiriza Ndinasunga uthenga wabwino wa madzi, mwazi ndi Mzimu m`mtima mwanga
Ndinadzindikira kuti kuli zinthu ziwiri zimene zimatipulumutsa, mdulidwe ndi mwazi a mwana wa nkhosa mu Chipangano Chakale ndi kuperekedwa kwa machimo onse pa Iye kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda mu Chipangano Chatsopano. Mdulidwe mu Chipangano Chakale ndi ubatizo wa Yesu mu Chipangano Chatsopano ndi zimodzidi ndiponso n’zofanana
Yesu Kristu anaweruzidwa osati chifukwa chakuti Iye anachita uchimo ulionse Iye Mwini, koma chifukwa anatenga machimo onse adziko kudzera mu ubatizo Wake. Onse amene akhulupilira kuti Yohane Mbatizi, ngati woimilira wa anthu onse, anabatiza Yesu ndi kupereka machimo onse adziko pa Yesu amakhulupiliranso muzonse mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda.
Kodi n’chifukwa chiyani anthu ambiri akukana ubatizo Wake ngakhale kuti ukufotokozedwa mu Baibulo mobwereza-bwereza? Mwa kuchita choncho, iwo ndi ochimwabe ngakhale kuti akukhulupilira mwa Yesu. Angakhulupilire mwa Yesu koma ndi okanidwabe kwa Mulungu. Ndi ochimwa omvetsa chisoni amene adzapitabe kugahena ngakhale kuti amakhulupilira mwa Yesu.
Kodi angakhale bwanji ochimwabe ngati akukhulupilira mwa Yesu? Kodi n’chifukwa chiyani akukhala ngati ochimwa? Kodi n’chifukwa chiyani akupita mnjira yachionongeko? N’zachisoni. Adzapitilizabe kukhala ochimwa chifukwa sakhulupilira choonadi chakuti machimo adziko onse anaperekedwa pa Yesu Kristu, amene anabweretsa chipulumutso chosatha ku anthu onse kudzera mu ubatizo Wake wa uzimu.
Anthu amaganiza kuti akuomboledwa mwa kukhulupilira mu mwazi wa Yesu, koma mtundu wa chikulupilirochi sichikuwapangitsa kukhala athunthu. Kodi n’chifukwa chiyani? Chifukwa analephera kupereka machimo awo pa Yesu!
Tingapulumutsidwe pokha mwa kukhulupilira mu madzi (ubatizo wa Yesu) ndi mu mwazi Wake m’njira imene Mulungu anasankha: chipulumutso cha mdulidwe wa mu uzimu. Ndiyeno, ndipo pokhapo, tingakhale ana oona a Mulungu.
Tiyenera kudzifunsa tokha. “Ngati tikhulupilira mu mwazi okha wa Yesu ngati mdulidwe wa uzimu, kodi machimo athu angatsukidwe mwathunthu?” Tiyenera kuyang’ana mkati mwa mitima yathu kuti tipeze yankho.
Mu Chipangano Chakale, anthu anapulumutsidwa kudzera mu mdulidwe ndi mwazi wa mwana wa nkhosa wa Paskha monga m`mene tikupezera chipulumutso mu ubatizo wa Yesu ndi mu mwazi Wake pa Mtanda. Mnjirayi tinapulumutsidwa kuchiweruzo cha Mulungu ndiponso kudzikoli lochimwa. Iwo amene akhulupilira amakhala ana a Mulungu ndipo Mulungu amakhala Tate wawo.
Munthu amapulumutsidwa ndikukhala m’modzi wa a Mulungu mwa kukhulupilira zinthuzi ziwirizi: mdulidwe ndi mwazi a mwana wa nkhosa wa Paskha, mwanjira ina, ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Ichi ndi choonadi malinga ndi Yesu. Ili ndi tanthauzo loona la kubadwa mwatsopano mwa madzi, mwazi ndi mwa Mzimu.
KODI CHIOMBOLO CHA MADZI NDI MZIMU CHOTCHULIDWA MU BAIBULO NDI CHIYANI?
Kodi ochimwa angakhale olungama mwa kukhulupilira mu mwazi a Yesu okha?
Nzosatheka
Yesu anasiya mpando Wake wa ufumu Kumwamba ndi kutsika pansi pano. Iye anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi pa msinkhu wa zaka makumi atatu (30) kuti achotse machimo onse adziko.
Mwazi wa Yesu pa Mtanda kunali kuweruzidwa Kwake chifukwa cha machimo a ochimwa onse a m’dziko. Yesu Kristu anabwera ngati Mpulumutsi kudzikoli ndipo anapulumutsa ochimwa onse kumachimo awo kudzera mu madzi ndi mwazi.
Kodi tinabadwa mwatsopano mwa mwazi okha? Ai. Timapulumutsidwa kuuchimo kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Ndifuna ndifunse funso ku aja amene akukhulupilira mu mwazi wa Yesu okha. “Kodi ochimwa angakhale olungama mwa kukhulupilira mu mwazi wa Kristu okha, kodi kapena ndi muzonse mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda? Kodi ndi mwa chikhulupiliro kuti tinapereka machimo athu pa Yesu kudzera mu ubatizo ndi mwazi Wake kapena ndi kudzera mu mwazi Wake okha? Kodi choonadi ndichiti, Ndikukufunsani?”
Kuti tibadwedi mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu, tiyenera kukwanilitsa zosatira. Tiyenera kukhulupilira kuti Yesu anabwera m’dzikoli mwa thupi, ndipo kuti Iye ananyamula pa Iye yekha machimo onse adziko pa Yordano kudzera mu ubatizo Wake ndipo anaweruzidwa chifukwa cha machimo athu onse pa Mtanda. Mwa kukhulupilira mwa Yesu Kristu, Mpulumutsi wathu oona, mnjirayi, tingabadwedi mwatsopano.
Ndikufunsaninso. Kodi chikhulupiliro ndi chiyani malingana ndi m`mene Baibulo likufotokozera? Kodi n’chikhulupiliro mu mwazi a Yesu, kapena muzonse mu ubatizo ndi mu mwazi Wake?
Chikhulupiliro mu mwazi wa Yesu chili motere: Yesu anaweruzidwa ndi kutsutsidwa chifukwa cha machimo onse adziko. Chifukwa Iye anakanthidwa ndi kulasidwa chifukwa cha machimo athu, tinapulumuka kuchiweruzo choopsa. Koma icho sichoona chathunthu. Tisanabvomere chiphunzitso ichi, tiyenera kukonzeratu mfundo yathu. Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anayenera kupachikidwa pa Mtanda?
Baibulo limaneneratu poyera kuti mphotho yauchimo ndi imfa. Yesu sanachite uchimo ulionse padzikoli. Iye anabwera m’thupi la munthu kudzera m’thupi la Maria, koma anabwera m’maonekedwe a chifaniziro cha anthu Ake ngati Mwana wa Mulungu Woyera ndiponso Mpulumutsi wa ochimwa. N’chifukwa chake Iye anayenera kubatizidwa ndi Yohane Mbatizi Iye asanafe pa Mtanda. Pamene Iye anabatizidwa ananyamula machimo anthu onse pa Iye yekha. Pachifukwa ichi, popanda ubatizo, Iye sakanazengedwa mlandu wokhetsa mwazi pa Mtanda.
MWAMBO WA KAPEREKEDWE KA NSEMBE MU CHIPANGANO CHAKALE
Kodi malamulo ofunikira pakupereka nsembe anali otani?
① Nyamba yamoyo yopanda chilema
② Kuika manja
③ Mwazi Ake
Tiyeni tione choonadi ichi kudzera mu mwambo wakupereka nsembe wa mu Chihema Choyera. Mu Chipangano Chakale, mwina ochimwa kapena wamkulu wansembe anali kuika manja pa mwana wa nkhosa woperekedwa sembe kapena pa mbuzi kuti apereke uchimo wake kapena machimo a Israyeli pa mutu wake. Nsembezo kenako zinali kuphedwa ndi kuperekedwa pa guwa. Chipangano Chakale chinali chithunzi cha Chipangano Chatsopano, ndipo Yesu Kristu anali mwana wa Nkhosa wa Mulungu amene analonjeza kutumiza.
Kodi ndiliti pamene nonsenu munapereka machimo anu onse pa Yesu? Ndifuna muganizirepo ndi kuyakha funsoli. Mu Chipangano Chakale, Aisrayeli sankapha nyama za nsembe popanda kuikapo manja (kuika manja chikutanthauza kupereka uchimo pa nsembe yauchimo). Nsembe zamachimo zisanabweretsedwe paguwa, kuikapo manja kunayenera kuchitika kuti apereke machimo pa nyamazo zoperekedwa nsembe.
“Ndipo aike dzanja lace pamutu pa nsembe yopsereza;” (Levitiko 1:4). Kunalembedwa mu Levitiko kuti nsembe zonse ziyenera kuikidwa manja. Mwakuika manja awo pamutu pansembe, anthu a Israyeli anatha kupereka machimo awo pamutu pa nsembeyo, ndipo mwa kupereka mwazi ndi nyama yake mwa chikhulupiliro pamaso pa Mulungu, iwo anali kupulumutsidwa kumachimo awo. Aisrayeli anali kupulumutsidwanso mwa chikhulupiliro m’nthawi ya Chipangano Chakale.
Pamene nsembe yopsereza inali kuperekedwa pamaso pa Mulungu, ochimwa anali kuika manja ake pamutu pa nsembeyo kuti apereke machimo ake a ochimwa. Kenako nsembeyo inali kuphedwa m’malo mwa ochimwa. Mwazi wake unapakidwa panyanga zinayi za guwa ndipo otsalawo anali kuthiridwa pansi patsinde laguwa. Umu ndi m`mene ochimwa anali kuomboledwera.
Mu Chipangano Chatsopano ochimwa angaomboledwe kumachimo awo onse kudzera mu chikhulupiliro chawo mu madzi ndi mwazi wa Yesu. 1 Yohane 5:1-10 ikuti ochimwa waomboledwa pamene akhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi a mwana wa nkhosa (Mtanda).
Choncho ochimwa aliyense angaomboledwe ngati akukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda. Ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, pamodzi ndi Mzimu Woyera, n’zofunikira kuti munthu abadwe mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.
Okondedwa, kodi mungaomboledwe mwa kukhulupilira mu mwazi a Yesu Kristu okha? Onse aja amene akuganiza kuti angabadwe mwatsopano mwa kukhulupilira mu mwazi okha a pa Mtanda ali ndi uchimobe m’mitima yawo. Koma tingapulumutsidwe kumachimo athu onse mwa kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ngati mdulidwe wa uzimu wa m’Chipangano Chatsopano, umene masiku ano ndi ofanana ndi mdulidwe ofotokozedwa mu Chipangano Chakale.
Mipingo yonse ili ndi ziphunzitso zawo. Tikudziwa kuti onse ayenera kupita kugahena ngati sasiya zikhulupiliro zawo zachinyengo. Malo a mpingo wa Presbyterian umakokomeza pa chiphunzitso chakusankidwa; mpingo wa Methodist umakokomeza pa chiphunzitso cha Arminias, monga,humanism; Baptist church, baptism; ndi Holiness church, holy life; onsewa anapatukako ku mawu oona.
Kodi nanga mawu oona mu Baibulo akunena chiyani za kubadwa mwatsopano? Baibulo likuti choonadi chikupezeka mu ubatizo wa Yesu ndi mu mwazi Wake. Wina aliyense amene akukhulupilira ndi kusatira mawu a Mulungu ndipo ali ndi chikhulupiliro mu kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu adzapeza chiombolo.
KODI CHINSINSI CHA UBATIZO WA YESU NDI CHIYANI?
Kodi mdulidwe wa uzimu mu Chipangano Chatsopano ndi chiyani?
Ubatizo wa Yesu
Ubatizo wa Yesu unali mdulidwe wa uzimu. Mu Chipangano Chakale, Mulungu anati wina aliyense amene sanadulidwe ayenera kuchotsedwa pa anthu Ake.
Tiyenera kudziwa ndi kukhulupilira kuti mdulidwe wa uzimu mu Chipangano Chatsopano ndi ubatizodi wa Yesu. Popeza Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi pachiyamba cha utumiki Wake wa poyera, tingadulidwe mu uzimu mwa kukhulupilira mu ubatizo Wake. Tiyenera kulingalilapo mosamala pachifukwa chimene Yesu anabatizidwira ndi Yohane Mbatizi.
“Pamenepo Yesu anacokera ku Galileya nadza ku Yordano kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye. Koma Yohane anati amkanize, nanena, ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi? Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti tiyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero. Pamenepo anamlola Iye.” (Mateyu 3:13-15).
Yesu anabadizidwa ndi Yohane Mbatizi mu Yordano, “mtsinje waimfa.” Yohane Mbatizi anaika manja ake pa mutu wa Yesu ndipo Iye anamizidwa mwathunthu. Iyi ndi njira yoyenera yobatizira (Ubatizo: kumizidwa mu madzi). Pofuna kuti Yesu atenge machimo onse adziko lonse, Iye anayenera kubatizidwa m’njira yomweyo, yakuikapo manja ya Mu Chipangano Chakale.
Ubatizo wa Yesu ndi mdulidwe wa mu uzimu kwa aja amene amakhulupilira mwa Yesu. “pakuti tiyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero.” (Mateyu 3:15). Kunali koyenera kuti Yesu atenge machimo onse a dziko ndi kukhala Mulungu ndi Mpulumutsi wathu. Motero, kunali koyenera, monga m`mene kunalembedwa, kuti Iye anafa pa Mtanda ndi machimo athu onse pa mutu Wake.
Ubatizo wa Yesu uli ndi mphamvu zopangitsa ochimwa onse kubadwa mwatsopano. Ndi chisinsi cha uthenga wa madzi ndi Mzimu.
Chinthu choyamba chimene Yesu anachita pa utumiki Wake wapagulu kuti apulumutse ochimwa kumachimo awo onse kunali kubatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Ubatizo ukutanthauza “kutsukidwa, kukwiriridwa, kupatsira.”
Pobatizidwa mnjira imene Mulungu anafuna, Yesu anatenga machimo onse adziko pa Iye yekha. “Onani mwanawankhosa wa Mulungu amene acosta cimo lace la dziko lapansi!” (Yohane 1:29). Ubatizo wa Yesu ukutanthauza kuti anthu onse a m’dziko amene akukhulupilira mwa Iye ndi odulidwa mu uzimu.
Pambuyo pake, Iye anapita pa Mtanda ngati Mwana wa nkhosa wa Mulungu amene anachotsa machimo onse adziko ndipo analandira chiweruzo cha ochimwa onse. Potero, Iye anapulumutsa anthu onse kumachimo awo.
Choncho, onse amene akukhulupilira mu ubatizo wa Yesu Kristu, mdulidwe wa mu Chipangano Chakale, ndi mwazi Wake pa Mtanda ngati chipulumutso chawo apulumutsidwa kumachimo awo onse. Yesu Kristu anapulumutsa ochimwa onse kupitira mu ubatizo Wake ndi mwazi Wake. Ichi ndicho choonadi cha mdulidwe wa uzimu.
KODI CHIPULUMUTSO NDI MWA MWAZI OKHA? AI, SI CHONCHO
Kodi Yesu anabwera padzikoli kudzera mwa chiyani?
Mwa madzi ndi mwazi
1 Yohane 5:4-8 ikuti, “Pakuti ciri conse cabadwa mwa Mulungu cililaka dziko lapansi; ndipo ici ndi cilako tililaka naco dziko lapansi, ndico cikhulupiriro cathu. Koma ndani iye wolilaka dziko lapansi, koma iye amene akhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu. Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, ndiye Yesu Kristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi. Ndipo Mzimu ndiye wakucita umboni, cifukwa Mzimu ndiye coonadi. Pakuti pali atatu akucita umboni, Mzimu, madzi ndi mwazi; ndipo iwo atatu ali mmodzi. ”
Okondedwa Akristu, kodi umboni wanu ndi chiyani wa Iye ngati Mpulumutsi wanu? Ndi chikhulupiliro mwa Mwana wa Mulungu amene anabwera mwa madzi ndi mwa mwazi.
Kodi chigonjetso chimene chikugonjetsa dziko ndi chiyani? Ndi mphamvu yachikhulupiliro mu madzi ndi mu mwazi. Ndi Yesu Kristu amene anabwera mwa madzi ndi mwa mwazi. Ndipo ndi Mzimu umene ukuchitira umboni, chifukwa Mzimu ndi choonadi.
Pali zitatu zimene zikuchitira umboni padziko: madzi mwazi ndi Mzimu. Ndipo atatuwa akuvomerezana ngati m’modzi. Yesu anabwera mu dzikoli mthupi, anabatizidwa ndi kufa pa Mtanda kutipulumutsa kuchionongeko chosatha. Umboni wakuti, Mulungu, Mlengi wathu, anakhala Mpulumutsi wa ochimwa onse ndi uthenga wa madzi ndi Mzimu umene umatipulumutsa ife tonse.
Ndi umboni wathu kuti Yesu, amene anabwera padzikoli ngati Mzimu mthupi, anabatizidwa mu Yordano kuti adzitengele pa Iye yekha machimo athu onse, ndipo anakhetsa mwazi pa Mtanda mwa kubvomera chiweruzo chifukwa cha machimo athu. Mwakutero, ndi m`mene Iye anapulumutsa onse amene akhulupilira mwa Iye. Uwu ndiwo uthenga wabwino woyamba wa madzi ndi Mzimu.
KODI MADZI NDI MWAZI AMENE AKUCHITIRA UMBONI WA CHIPULUMUTSO CHA MULUNGU NDI CHIYANI?
Kodi chofanana ndi mdulidwe ofotokozedwa mu Chipangano Chakale ndi chiyani?
Ubatizo wa Yesu
Madzi akuimilira ubatizo wa Yesu Kristu. Mu Chipangano cha Kale, ubatizo wa Yesu unali kutanthauza mdulidwe. Chogwirizana ndi mdulidwe wa mu Chipangano cha Kale ndi ubatizo wa Yesu mu Chipangano Chatsopano. Chitsimikizo chakuti machimo onse anaperekedwa pa Yesu chili mu ubatizo wa Yesu.
Aliyense amene akukhulupilira mu choonadi ichi akhoza kuimilira pamaso pa Mulungu ndi kunena mwa chikumbumtima cha bwino, “Ndinu Mpulumutsi wanga, Mbuye wanga chifukwa Ndikhulupilira mu ubatizo Wanu ndi mu mwazi Wanu, uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Pacifukwa ichi, Ndilibe uchimo. Ndine mwana wa Mulungu ndipo Ndinu Mpulumusi wanga.” Tinganene izi mwa chikhulupiliro choona. Chifukwa chimene tikhoza kunena izi ndi chifukwa cha chikhulupiliro chathu mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake.
Kodi ndi mawu otani amene amatilora kuti tibadwe mwatsopano? Ndi ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake pa Mtanda, umene ndi umboni wa chipulumutso chathu m`mitima yathu. Uwu ndiwo uthenga wabwino wakubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.
Okondedwa Akristu, Ndikufunsaninso, “Kodi ochimwa angapulumutsidwe mwathunthu kupitira mu chikhulupiriro cha mwazi wa Kristu okha?” Ai. Chipulumutso sichikufuna chikhulupiliro mu imfa Yake yokha pa Mtanda. Koma ndi kudzera mu chikhulupiliro mu madzi ndi mu mwazi —uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu—kotero kuti ochimwa angabadwe mwatsopano. Lekani tsopano ndikuonetseni mu Baibulo tsopano, pamene akukamba za madzi kapena munjira ina ubatizo wa Yesu.
1 Petulo 3:21-22 ikuti, “Cimenenso cifaniziro cace cikupumutsani tsopano, ndico ubatizo, kosati kutaya kwa litsoro lace la thupi, komatu funso lace la cikumbu mtima cokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Kristu; amene akhala pa dzanja lamanja la Mulungu, atalowa m’Mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zomgonjera.”
Mtumwi Petro akuchitira umboni kuti ubatizo wa Yesu ndi chifaniziro chimene chimatipulumutsa ife, ndi chitsimikizonso cha chipulumutso ku uchimo. Ubatizo wa Yesu ukufanana ndi mdulidwe wa mu Chipangano Chakale. Monga momwe anthu a Israyeli anakhulupilira mu mawu a Mulungu ndi kudula khungu lawo la kusonga kuti akhale ana a Mulungu m’nthawi ya Chipangano Chakale, ubatizo wa Yesu umatipulumutsa ku machimo athu onse m’nthawi ya Chipangano Chatsopano.
Choncho mdulidwe mu Chipangano Chakale ndi ubatizo wa Yesu mu Chipangano Chatsopano ndi chimodzi-modzi ndipo n’zofanana. Kodi nonsenu tsopano mukukhulupilira kuti ubatizo wa Yesu ndi chimodzi-modzi ndi mdulidwe? Monga kunalembedwa mu 1 Petro 3:21, chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho ubatizo. Kodi mungatsutsane ndi mawu olembedwa a Mulungu?
Kodi chilibwanji kuti ife, amene tikukhala m’dzikoli, tingamasulidwe bwanji ku uchimo? Ndi chifukwa chakuti Yesu anabatizidwa kuti akwaniritse chilungamo chonse mwakuti chipulumutso ku uchimo chikupezeka kwa ife. Mateyu 3:15 ikuti, “Pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero.”
Chifukwa machimo onse adziko anaperekedwa pa Yesu, onse amene okhulupilira mwa Iye alibe uchimo. Tonse tingakhale olungama mwa kukhulupilira kuti machimo athu onse anaperekedwa pa Yesu kudzera mu ubatizo Wake. Yesu Kristu anatenga machimo athu onse pa Iye yekha ndipo anafa pa Mtanda kuti atipulumutse kuchiweruzo chonse.
Okondedwa abwenzi, zinthu ziwiri zimene zimapulumutsa ochimwa onse kumachimo awo ndi madzi ndi mwazi. Kutenga Kwake kwa machimo athu ndi kufa Kwake pa Mtanda chifukwa cha ife ndi zinthu ziwiri zeni-zeni zimene Yesu anatichitira mzaka zitatu utumiki Wake wapagulu mdzikoli.
Yohane 1:29 ikuti, “Onani mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” Yesu Kristu anabatizidwa kuti achotse uchimo wa dziko ndipo anafa pa Mtanda kuti atetezere zolakwa zathu. Yesu ndi Mwana wa Mulungu, ndipo ngati Mlengi, anakwaniritsa chipangano cha mdulidwe chimene Mulungu anapanga mu Chipangano Chakale mwa kuchotsa machimo adziko.
Aliyense amene akukhulupilira m’mtima mwake uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu, madzi ndi mwazi adzabadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Ndipo Ambuye adzakhala Mpulumutsi wa onse amene amakhulupilira. Thokozani Ambuye, Aleluya! Yesu anakwaniritsa chipulumutso chathu monga m’mene Mulungu analonjezera, ndipo Iye anatipulumutsa kumachimo onse adziko.
KOSATI KUTAYA LITSIRO LACE LA THUPI
Kodi thupi limayeretsedwa mwa nthawi?
Ai. Thupi limapitiliza kusonkhanitsa uchimo mpaka patsiku lakufa.
1 Petro 3:21 ikuti, “Cimenenso cifaniziro cace cikupumutsani tsopano, ndico ubatizo, kosati kutaya kwa litsoro lace la thupi, komatu funso lace la cikumbu mtima cokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Kristu.”
Ngati wina wabwera kukhulupilira mwa Yesu ngati Mpulumutsi wake, sichitanthauza kuti iye wasiya kuchita uchimo wa thupi. Tingapitirize kuchimwa, koma mwa kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu, tingapereke machimo athu onse adziko kwa Yesu, amene anawalipilira mwa mwazi Wake pa Mtanda. Mwakukhulupilira mu zinthu ziwirizi ngati zinthu ziwiri zofunika kwambiri pa chipulumutso chathu, tinapulumutsidwa kumachimo athu.
Kubadwa mwatsopano chitanthauza kulandira Yesu m’mitima yathu ngati Mpulumutsi wa anthu onse. Chikhululukiro cha uchimo nachonso chinakwaniritsidwa m`mitima yathu. Ngati tikukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda, mitima yathu inabadwa mwatsopano, Koma tikupitirizabe kuchita uchimo ndi zolakwa ndi matupi athu. Koma, machimo a thupi lathu onse anakhululukidwa kale.
Ubatizo wa Yesu ndi umboni kwa onse aja amene anapulumutsidwa. Tilibe uchimo ngati tikukhulupilira mu chikhululukiro cha uchimo kudzera mu ubatizo wa Yesu. Tikubadwa mwatsopano ngati tilandira m’mitima yathu choonadi cha chipulumutso kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi kukhala olungama kudzera mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Ichi ndi chikhulupiliro cha Abrahamu mu Chipangano Chakale, chikhulupiliro chakukhala olungama cha cimene Mtumwi Paulo analankhulapo, ndi chifaniziro cha chipulumutso chimene mtumwi Petro anachitira umboni.
Monga m’mene Abrahamu anamva ndi kukhulupilira mu mawu a Mulungu ndi kukhala olungama, tikupulumutsidwa ngati takhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi imfa Yake pa Mtanda.
Yohane 1:12 ikuti, “Koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lace.” Kodi mwalandira Yesu Kristu, Amene anatipulumutsa kumachimo athu onse kupitira mu ubatizo ndi mwazi wake, ngati Mpulumutsi wanu? Tiyenera kulandira chipulumutso chopatsidwa kwa ife kudzera mu madzi ndi mwazi wa Yesu.
Kodi chipulumutso ndi mwa mwazi wa Yesu okha? Ai. Ndi mwa madzi ndi mwazi wa Yesu. Mu Baibulo, kunalembedwa molondola kuti chipulumutso si mwa mwazi wa Yesu okha. Ndi mwa ubatizo wa Yesu ndi mwa mwazi Wake.
Ubatizo wa Yesu ndi mdulidwe wa uzimu mu Chipangano Chatsopano. Ndi choonadi cha chipulumutso chimene chimadula machimo athu onse kwa ife. Choona chakuti Iye anawerudzidwa chifukwa cha machimo adziko chikutanthauza kuti Iye anaweruzidwa chifukwa cha ife, inu ndi ine.
Mwakulandira uthenga wabwino wachikhululukiro chamachimo, ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, tinamasulidwa kuchiweruzo cha machimo athu. Mwa chikhulupiliro chathu, tikupulumutsidwa kumachimo onse tikuchita mdzikoli. Tikatenga ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake ngati chipulumutso chathu, machimo onse m’mitima yathu atsukidwa. Kodi mukukhulupilira ndi kumvetsetsa izi ngati zoona? Ndikukhulupilira kuti nonse mudzakhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Khulupilirani ndipo mupeze umoyo osatha.
Mtumwi Paulo anati, “ndipo mdulidwe uli wa mtima” (Aroma 2:29). Kodi tikudulidwa bwanji mu mtima wathu? Tingadulidwe mu Mzimu ngati takhulupilira mu kubwera kwa Yesu Kristu padzikoli mthupi, mu ubatizo Wake kuti achotse machimo onse adziko, mu imfa Yake pa Mtanda cifukwa cha machimo athu, ndiponso mkuukitsidwa Kwake kwa akufa.
Mtumwi Paulo anati mdulidwe ndi wa mtima. Mdulidwe wa mtima ukutanthauza kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Ngati mufuna kudulidwa mu mtima mwanu, muyenera kuika uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake mu mtima mwanu. Ndiyeno, pokhapo, mungakhaledi ana a Mulungu.
KODI YOHANE MBATIZI ANATUMIDWA NDI MULUNGU?
Kodi Yohane Mbatizi anali Ndani?
Iye anali mtumwi wa anthu Ndiponso wamkulu wansembe omaliza malingana ndi pfuko la Aroni.
Apa, tikufunika kuti tifunse za Yohane Mbatizi amene anabatiza Yesu Kristu. Yohane Mbatizi anali mtumwi ya anthu onse. Mateyu 11:11-14 ikuti, “Indetu ndinena kwa inu, sanauke wakubadwa mwa akazi munthu wamkuru woposa Yohane Mbatizi; koma iye amene ali wocepa mu Ufumu wa kumwamba amkulira iye. Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa kumwamba uli wokangamizidwa, ndipo okangamirawo aukwatula ndi mphamvu. Pakuti aneneri onse ndi cilamulo cinanenera kufikira pa Yohane. Ndipo ngati mufuna kulandira, uyu ndiye Eliya amene amati akudza”
Okondedwa Akristu, Yesu akuti kulibe wamkulu woposa Yohane Mbatizi pakati pa obadwa mwa akazi. Ndikubadwa kwa Yohane Mbatizi, nthawi ya Pangano Loyamba la Mulungu, nthawi ya Chipangano Chakale inatha. Inatha chifukwa Yesu Kristu amene anayenera kukwaniritsa pangano la Mulungu anabwera pomaliza.
Kodi iyeyo anali ndani tsopano, amene anali kuyenera kukwaniritsa pangano la Mulungu? Yesu Kristu ndi Yohane Mbatizi. Yohane Mbatizi anapereka machimo onse adziko pa Yesu. Kodi ndi ndani amene anali wansembe wamkulu womaliza wa mu Chipangano Chakale? Kodi ndi ndani anali wapfuko la Aroni? Yesu Kristu Iye yekha anachitira umboni kuti anali Yohane Mbatizi. Yohane Mbatizi anali ntumwi wa anthu onse, wamkulu woposa onse wobadwa mwa akazi.
Tiyeni tiganizire pa zoona zimene tili nazo. Mose, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo onse anali obadwa kwa akazi. Koma pakati pa anthu onse mu Chipangano Chakale ndi Chatsopano, kodi wamkulu ndani pakati pa onse obadwa kwa akazi? Ndi Yohane Mbatizi.
Yohane Mbatizi, monga mneneri womaliza wa mu Chipangano Chakale ndiponso wa m’banja la Aroni, anabatiza Mwana wa nkhosa wa Mulungu mu Chipangano Chatsopano m’njira yofanana imene Aroni anali kuika manja ake pa nsembe zopsereza pa Tsiku La chitetezero cha machimo mu Chipangano Chakale. Iye anabatiza Yesu Kristu ndi kupereka machimo onse adziko pa Yesu. Iye anali mtumiki wa Mulungu. Iye anakwaniritsa mdulidwe wa uzimu m’mitima ya anthu onse mwa kubatiza Yesu Kristu.
Pamodzi ndi ubatizo wa Yesu, tiyenera kukhulupilira mu mwazi Wake ngati umboni wachipulumutso chathu. Yesu Kristu anachotsa machimo onse a dziko kudzera mu ubatizo Wake ndipo anaweruzidwa chifukwa cha machimowo. Ndipo chinthu chimene tiyenera kuchita chokhacho ndi kukhulupilira mu zimenezi. Ndichifuniro cha Mulungu kuti ife tikhulupilire mu chimene Yesu anachitira.
Pamene mwatenga mu mtima mwanu uthenga wabwino wakubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu, mungakhale wapfuko la Abrahamu ndiponso mwana wa Mulungu. Kuli ang’ono chabe amene ali mwa Kristu pamene kuli ambiri amene sanamubvomereze Iye m’mitima yawo.
Tsiku lili pafupi kutha ndipo mdima wafika. Khulupilirani mu ubatizo wa Yesu ndipo muloleni Iye kuti alowe mu mtima mwanu. Chikhulupiliro chanu mu ubatizo wa Yesu ndi mu magazi Ake chidzakupanga kuti mudalitsike ndi chipulumutso cha uzimu.
sungani mu nzeru zanu matsiku onse kuti kudzodzedwa kwa uzimu kumabwera pamene mwakukhulupilira mu uthenga wabwino wa chipulumutso, uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Ndikufuna inu mudziwe kuti mungakonze nyali ya mu uzimu (Mpingo) ndi mafuta (mzimu) ngati anamwali ochenjela (Mateyu 25:4) mwa kukhulupilira mu uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Aja amene amakhulupilira mwa Yesu amapita ku kachisi ali ndi Mzimu m`mitima yawo.
KODI N’CHIFUKWA CHA NDANI YESU ANABATIZIDWA?
Kodi ndi pacholinga chotani chimene Yesu anabatizidwira?
Kuti achotse machimo onse a anthu
“Koma Yohane anati amkanize, nanena, ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, mudza kwa ine kodi? Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero.” (Mateyu 3:14-15).
Yesu anabatizidwa kuti achotse machimo a anthu onse. Yesu Kristu ndi Mwana wa Mulungu ndiponso ndi Mpulumutsi wathu. Iye ndi Mlengi amene anatipanga ife. Yesu Kristu anabwera mwa chifuniro cha Mulungu, Atate, kuti azapange ife kukhala anthu Ake.
Kodi aneneri a mu Chipangano Chakale anali kulankhula za ndani? Anali kulankhula za Yesu Kristu. Aneneri onse a mu Chipangano Chakale anali kulankhula zakubwera kwa Yesu mdzikoli kudzachotsa machimo onse ndi kutimatsula ife ku uchimo kwamuyaya.
Yesu anabwera padzikoli monga m`mene ananenera mu Chipangano Chakale ndipo anachotsa machimo onse a anthu kuyambira kwa Adamu ndi Hava kufikira kumunthu adzatsilizira kukhala padziko.
Tsopano, ikani m’mitima yanu chipulumutso kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Kodi mukukaikirabe kuti ichi ndi choonadi? Kodi mukali ndi uchimo m’mtima wanu? “Pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero.” Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi kuti akwaniritse chilungamo chonse.
Liwu lakuti “ubatizo” lokha likutanthauza “kutsukidwa.” Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi m’njira yakuikapo manja yofotokozedwa mu Chipangano Chakale.
Atatenga machimo onse a anthu, Iye anazimiza Iye yekha mu Yordano. Mtsinje ukutanthauza imfa ndi chiweruzo cha ochimwa. Kumizidwa kwa Yesu m’madzi kuwonetsa imfa Yake pa Mtanda. Kuvuuka kwake m’madzi kuwonetsa kuuka Kwake kwa akufa. Yesu anautsidwa patsiku lachitatu atafa pa Mtanda.
Yesu ndi Mulungu ndiponso M’pulumutsi wathu. Choona chakuti Yesu anabwera padzikoli kuti abatizidwe, kukhetsa mwazi mpaka kufa pa Mtanda, anaukitsidwa patsiku lachitatu, ndipo tsopano akukhala kudzanja lamanja la Mulungu ndi umboni wolondola kuti Iye anapulumutsa anthu onse kuimfa. Kodi mkukhulupilira kuchoka pansi pa mtima wanu mu choonadi ichi?
Ubatizo wa Yesu ndi mdulidwe wa mu uzimu mu Chipangano cha Tsopano. “Ndipo mdulidwe uli wa mtima.” Mdulidwe wa m’mtima umakwaniritsidwa ngati tikukhulupilira mu ubatizo wa Yesu, choonadi chakupereka machimo onse kwa Yesu. Mdulidwe wa mtima ndi kuzindikira kwa ubatizo wa Yesu kudzera mu umene tikuperekera machimo athu onse pa Yesu.
Kodi munadulidwa mu mtima mwanu? Ngati mukukhulupilira mu mdulidwe wa mu mtima mwanu, machimo anu adzachotsedwa kamodzi kokha. Chifukwa cha cholinga ichi Yesu anakwaniritsa chilungamo chonse ndipo anatsimikizira chipulumutso cha ochimwa onse.
Okodedwa Akristu, sungani chitsimikizo ichi cha chipulumutso m’mitima yanu ndi maganizo anu. Ichi ndi choonadi. Mukangosunga mu mtima mwanu chipulumutso cha Yesu, mudzamasulidwa kumachimo anu onse. “Koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lace” (Yohane 1:12).
Kodi mukuona tsopano chifukwa chimene Yesu anabwerera padzikoli kuti adzabatizidwe? Kodi mukukhulupilira zimenezi tsopano? Yesu anabatizidwa kuti achotse machimo a anthu onse. Unali ubatizo wa mdulidwe. Ubatizo wa Yesu ukutipatsa mdulidwe wa mu uzimu. Icho ndicho chifukwa Mtumwi Paulo akutiuza kuti tidulidwe m`mitima yathu. Yesu anatipulumutsa molondola kwambiri ndi ubatizo Wake ndi mwazi kotero kuti tilibe chisankho koma kukhulupilira mu izi m’mitima yathu. Tiyenera kunena “Inde. Amee” ku mawu a Mulungu m`mitima yathu. Kodi ichi si choonadi? Kodi mkukhulupilira mu chimenechi?
KODI MUKUBVOMERA CHOONADI ICHI MU MTIMA MWANU?
Kodi tiyenera kuchita chiyani, tisanalambire Yesu?
Tiyenera kuika m`mitima yathu choonadi cha madzi ndi mwazi.
Pafupi-fupi zaka zikwi ziwiri (2000) zapita kuchokera pamene Yesu anabwera padzikoli. Tsiku lalero ndi m’nthawi ino yachisomo cha Mulungu, tiyenera kusunga m’mitima yathu choonadi, madzi ndi mwazi wa Yesu. Kulibe china chilichonse chimene ife tingachite.
“Ndipo mdulidwe uli wa mtima” Tiyenera kudulidwa kudzera mu chikhulupiliro chathu m`mitima yathu. Tingapulumutsidwe kudzera mu chikhulupiliro chokha. Mu Chipangano Chakale, Aisrayeli anapulummutsidwa kudzera mu mdulidwe ndi mwazi wa Paskha umene unapakidwa ndi pa mphuthu za nyumba zawo.
Onse aja amene akukhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu ngati chipulumutso chawo alibe mantha ndi chiweruzo cha Mulungu chifukwa chidzawapitilira. Koma chiweruzo cha Mulungu chidzagwera pa onse amene saika choonadi m’mitima yawo. Kuli ambiri amene akukhulupilira mwa Yesu pachabe ndipo ndi akapolobe a machimo awo.
Kodi iwo anafika bwanji pamenepa? Kodi n’chifukwa chiyani akubvutikabe ndi uchimo? Ndi chifukwa chakuti sadziwa choonadi cha ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Amakhulupilira mu mwazi wa Yesu okha, kusiya kapena kunyaranyaza ubatizo Wake.
Kodi chipulumutso chikupezeka kudzera mu chikhulupiliro chophweka cha mwazi wa Yesu okha? Kodi Baibulo limatiuza kuti ichi chiri chonchi? Kodi Chipangano Chakale ndi Chatsopano chikunena chiyani za zimenezi? Malingana ndi Baibulo, si mwa mwazi wa Mwana wa nkhosa wa Mulungu okha, koma ndi mwa ubatizonso wa Yesu kotero kuti chipulumutso chikupezeka (1 Yohane 5:3-6).
Kodi mumakhulupilira mu mwazi wa Yesu okha? Onse aja amene akukhulupilira chonchi ayenera kukhalabe ndi uchimo m`mitima yawo. Ayenera kugonjetsa chikhulupiliro chawo cholakwika ndi kubwelera ku uthenga wabwino weniweni.
Onse aja amene sakhulupilira tsopano ayenera kuzindikira kuti anasochera, posadziwa kuti Yesu anachotsa uchimo wonse pa Yordano kudzera mu ubatizo Wake. Ayenera kuvomera kuti anali kulakwa posaubvomera ubatizo wa Yesu. Ayenera kuchitenga m`mitima yawo kuti Yesu anachotsa machimo onse adziko kudzera mu ubatizo Wake. Chipulumutso chilipo ngati tangokhulupilira muzonse mu ubatizo wa Yesu ndi mu Mtanda Wake. Mwanjira ina, kudzera mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu okha tikhonza kupeza moyo osatha.
Okondedwa Akristu, kodi mwakhala moyo mpaka tsopano kudalira mu chikhulupiliro cha mwazi wa Yesu okha? Ngati zili choncho, ndithudi, muli ndi uchimo mu mtima mwanu. Ngati mukuchimwa, ndiye kuti muli ndi uchimo mu mtima mwanu. Ngati mukuganiza kuti ndinu omasulidwa ku uchimo wanu pamene mukukhala mwa lamulo la Mulungu, ndiye kuti ndi kumasuka chabe kumene kumachoka kumaganizo anu. chitsimikizochi sikugwirizana ndi mawu a Mulungu.
NTHAWI SINATHEBE
Kodi chonadi chimatimasura kuchiyani?
Kuchoka kuchilamulo cha uchimo ndi imfa
Nthawi sinathebe. Chimene muyenera kuchita ndi kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mu mwazi Wake, ndipo mudzadulidwa mu mtima mwanu ndi kumasulidwa kuuchimo wonse. Kumasulidwa kumachimo onse zikutanthauza kuti munapulumutsidwa mwa kukhulupilira mu uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake.
Kodi mufuna kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake kuti mupulumutsidwe kumachimo anu? Pokhapo ngati mwa mwakhulupilira mu izi, mudzaphunzira m`mene chipulumutso chilili. Mdzalandira mtendere wa m’mtima. Ndiyeno, ndipo pokhapo, mudzakhala olungama. Osati kupitira mu ntchito zanu, koma kudzera mu chikhulupiliro chanu mu mawu a Mulungu. Ngati wina wa inu akukhulupilirabe mu ndi kudalira mu mwazi okha a Yesu pa chipulumutso, Ndikufuna ndikulimbikitseni kuti khulupilirani muzonse mu ubatizo wa Yesu ndi mu mwazi Wake.
Okondedwa Akristu, Chipulumutso chathunthu cha anthu kuuchimo chinakwanilitsidwa kupitira mu uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Mzimu ndi Mulungu. Mulungu anabwera padzikoli mu thupi la munthu.
Mulungu anayankhula kudzera mwa aneneri kuti timutche dzina lake Yesu, chifukwa Iye adzapulumutsa anthu Ake kumachimo. Mulungu anati, “Onani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, ndipo adzamucha zdina lace, Emanueli; ndipo losandulika, Mulungu nafe” (Mateyu 1:23).
Mulungu anabwera pansi pano kudzapulumutsa ochimwa. Iye anabatizidwa kuti achotse machimo onse adziko ndipo mwakutero anapulumutse ochimwa onse. Ichi n’choonadi ndi chipulumutso cha madzi ndi mwazi. Ndilipano kukuuzani izi. Kodi tinapulumutsidwa kudzera mu mwazi wa Yesu okha? sichoncho ai. Tinapulumutsidwa mwa ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake pa Mtanda.
Kuli aneneri ambiri onyenga ndi ampatuko masiku ano amene sakhulupilira mu ubatizo wa Yesu. Yesu anati, “Ndipo mudzazindikira coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani” (Yohane 8:32).
Tiyenera kudziwa choonadi. Tiyenera kudziwa chifukwa chimene Yesu anakambira za ubatizo Wake, ndipo n’chifukwa chiani tiyenera kukhulupilira mwa iwo. Tiyenera kudziwa chifukwa chimene Mulungu anaudzira anthu a Israyeli kuti adzidulidwa mu Chipangano Chakale ndi chifukwa chimene Iye analankhulira za mwazi mwana wa nkhosa wa Paskha.
Ngati tadziwa mbali imodzi yokha ya nkhani, sitingazindikire choonadi. Yesu anati, “Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu” (Yohane 3:5).
KUBATIZIDWA MWA KRISTU
Kodi tingayanjane bwanji ndi imfa ya Kristu?
Mwa kupereka machimo athu onse pa Yesu kudzera mu ubatizo Wake.
Baibulo likuchitira umboni wachinsinsi cha chipulumutso. Kodi ndi mwa mwazi wa Yesu okha? Ai. Ndi mwa mwazi ndi mwa ubatizo Wake zonse pamodzi. Mtumwi Paulo analankhula zaichi kawirikawiri mu Aroma ndime ya 6 ndiponso mu makalata ake ena ambiri.
Tiyeni tiwerenge Aroma 6:3-8. “Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwa Kristu Yesu; tinabatizidwa mu imfa yace? Cifukwa cace tinaikidwa m’manda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo kulowa muimfa; kuti monga Kristu anaukisidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, cotero ifenso tikayende m’moyo watsopano. Pakuti ngati ife tinakhala olumikizidwa ndi Iye m’cifanizidwe ca imfa yace, koteronso tidzakhala m’cifanizidwe ca kuuka kwace; podziwa ici, kuti umunthu wathu wakale unapacikidwa pamodzi ndi Iye, kuti thupilo la ucimo likaonongedwe, kuti ife tisakhalenso akapolo a ucimo; pakuti iye amene anafa anamasulidwa kuucimo. Koma ngati ife tinafa ndi Kristu, tikhulupirira kuti tidzakhalanso amoyo ndi Iye.”
Tiyeni tiwone m’ndime ya 5. Imene ikuti, “Pakuti ngati ife tinakhala olumikizidwa ndi Iye m’cifanizidwe ca imfa
yace, koteronso tidzakhala m’cifanizidwe ca kuuka
kwace”
Imfa yake inali imfa yathu chifukwa machimo athu onse anaperekedwa pa Iye kudzera mu ubatizo Wake. Chotero ubatizo wa Yesu umatiyanjanitsa ife ndi mwazi wake pa Mtanda
Chikhulupiliro chathu mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake chikutilora kuti tilumikizane ndi Yesu. “Pakuti mphotho yace ya ucimo ndi imfa” (Aroma 6:23). Choncho imfa ya Yesu pa Mtanda inali imfa yathu. Iye anabadizidwa kuti atenge machimo athu onse pa Iye yekha. Kukhulupilira mu choonadi ichi ndi kuzilumikiza ife tokha ndi Yesu Kristu, Mpulumutsi wathu.
SITIYENERA KUKHULUPILIRA MWA YESU MOPHWEKA CHABE NGATI NJIRA YA CHIGAWO CHA CHIPEMBEZO
Kodi zikutanthauza chiyani kuti “Iye ndi wokhulupirika komanso wolungama?”
Zikutanthauza kuti Yesu anachotsa machimo athu kamodzi kokha ndipo wapulumutsa wina aliyense amene akukhulupilira mu choonadi.
Anthu ambiri amakhulupilira mwa Yesu ngati njira ya umoyo wachipembezo, chotero amapita kukachisi ndi kulira misozi popemphera ndi kulapa. Amaulura machimo awo ndi kupempha chikhululukiro tsiku ndi tsiku, Amapemphera, “Yesu, Ndidziwa ndi kukhulupilira kuti Inu munandifera pa Mtanda. Inde, Ndikhulupilira.”
Poyera, samvesetsa ndime yosatirayi. “Ngati tibvomereza macimo athu, ali wokhulupirira ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire macimo athu, ndi kutisambitsa kuticotsera cosalungama ciri conse.” (1 Yohane 1:9). Amanena kuti ayenera kukhululukidwa machimo awo tsiku ndi tsiku mwa kuvomereza uchimo wawo. Koma uchimo wa m’ndime yapamwambayi si ukutanthauza zolakwa zazing’ono za tsiku ndi tsiku. Chimene ndime ikutanthauza n’chakuti timakhululukidwa ku machimo athu kamodzi kokha ngati tavomereza kuti sitinapulumutsidwebe.
“Comweco cikhulupiriro cidza ndi mbiri, ndi mbiri idza mwa mau a Kristu.” (Aroma 10:17). “Ndipo mudzazindikira coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani” (Yohane 8:32).
Okondedwa Akristu, Choonadi chili poyera. Ngati mukukhulupilira kuti Yesu anafa pa Mtanda popanda kuchotsa machimo athu onse kudzera mu ubatizo Wake mu Yordano, chikhulupiliro chanu ndi chopanda pake. Ngati Mkristu aliyense afuna kupulumutsidwa kumachimo ake onse, ayenera kukhulupilira kuti machimo ake anaperekedwa pa Yesu kudzera mu ubatizo Wake mu Yordano kamodzi kokha ndi kuti Iye anatenga chiweruzo cha machimo athu onse pa Mtanda. Mwanjira ina, tiyenera kukhulupilira muzonse mu ubatizo wa Yesu ndi mu mwazi Wake.
“Ndipo palibe cipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.” (Macitidwe a Atumwi 4:12). Yesu Kristu anatenga machimo athu onse kudzera mu ubatizo Wake ndipo anakhala Mpulumutsi wathu. Yesu anabwera mwa madzi ndi mwa mwazi kuti atipulumutse kuchionongeko chosatha. “Pakuti ndi mtima munthu akhulupira kutengapo cilungamo; ndi mkamwa abvomereza kutengapo cipulumutso” (Aroma 10:10). Kodi ndiwe wochimwa kapena munthu wolungama?
Agalatiya 3:27 ikuti, “Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Kristu mudabvala Kristu.” Ndimeyi ikutiuza choonadi chakuti Yesu anapachikidwa pamene anatenga machimo onse adziko kudzera mu ubatizo Wake. Iye anaukitsidwa kwa akufa patsiku lachitatu ndipo tsopano akukhala kuzanja lamanja la Mulungu. Iye anakhala Ambuye wachipulumutso wa onse aja amene akhulupilira mwa Iye.
Kukanakha kuti Yesu sanabatizidwe, ndiponso kuti Iye sanakhetse mwazi wake pa Mtanda chifukwa chaife, Iye sakanakhala Mphulumutsi wathu. Tingapulumutsidwe pokhapo ngati tikukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
NGAKHALENSO MWANA WA MOSE
Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu anafuna kupha Mose m’njira yake yaku Igupto?
Chifukwa iye sanadule ana ake amuna
Okondedwa apamtima, mukumvera chisinsi chakuomboledwa kwa machimo anu onse kudzera mu madzi ndi mwazi wa Yesu. Ndi dalitso lodabwitsa kumvetsera mauwa a Mulungu.
Kodi ndi mwazi wa Yesu Kristu okha? M’nthawi ya Chipangano Chakale, Anthu anali kukhala afuko la Abrahamu kudzera mu mdulidwe ndi mu mwazi wa mwana wankhosa wa Paskha. Tsopano tinakhala anthu a Mulungu mwa kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake. Mulungu anationetsa umboni wa izi mu Chipangano Chakale kudzera mwa Mose.
Kuti apulumutse anthu a Israyeli, Mulungu anakamba ndi Mose ndi kumuuza kuti atulutse anthu Ake ku Igupto. Chotero Mose, mwa chilorezo cha mpongozi wake Yetero, anasiya dziko la Amidiya ndi kupita ku Igupto pamodzi ndi mkazi wake ndi ana ake aamuna. Pamene anakwezeka banja lake pa bulu, Ambuye anakumana naye pamsasa ndipo anafuna kumupha.
Koma mkazi wake wanzeru Zipora anadziwa chifukwa chake cha izi. Anatenga mwala wakuthwa ndi kudula khungu la kunsonga kwa mwana wake wa mwamuna ndi kuliponya pamapazi a Mose ndipo anati, “Pakuti iwe ndiwe mkwati wanga wamwazi.” Choncho Mulungu amusiya kuti apite.
Iyi inali njira Yake yakunena kuti Iye adzaphadi aliyense ngakhale mwana wa Mose, ngati sanali odulidwa. Ku anthu a Israyeli, mdulidwe unali chizindikiro chapangano la Mulungu. Anali kudziwa kuti moona Mulungu azadula aliyense kuchoka ku anthu Ake, ngakhale mwana wamtsogoleri, ngati wakhalabe osadulidwa. Pacifukwa ichi, kupewetsa kudula mwana wake, Mulungu anamudziwitsa Mose m’njirayi.
Baibulo limanena kuti chifukwa chimene Zipora anadulira khungu la mwana wake ndi kuliponya pamapazi a Mose n’kunena “Pakuti iwe ndiwe mkwati wanga wamwazi.” kunali kuvomereza kufuna kwa Mulungu kwa mdulidwe (Eksodo 4:26).
Wina aliyense amene sanali odulidwa pakati pa Aisrayeli anali kudulidwa ku anthu Ake. Okhawo odulidwa anali kuloledwa kudya nyama ya mwana wankhosa wa Paskha ndi kulowa mu mapemphero ngati anthu a Mulungu.
Mtumwi Paulo anali Mhebri. Anadulidwa patatha masiku asanu ndi atatu atabadwa, anaphunzira pansi pa mphunzitsi wamkulu, Gamalieli, ndipo anamvetsetsa ndendende chifukwa chimene Yesu Kristu anabatizidwira mu Yordano komanso chifukwa chimene Iye anayenera kupachikidwa. Pachifukwa ichi Mtumwi Paulo analemba za ubatizo wa Yesu mu Makalata ake onse.
Mtumwi Paulo analankhulanso za mwazi wa Yesu ngati chokwanilitsa chipulumutso chathu. Mwazi unali ntchito yomaliza ya chiombolo Chake pamene mdulidwe wa mu uzimu unali ubatizo wa Yesu. Sichithandiza kungokamba za mwazi wa Yesu popanda ubatizo Wake.
Mtumwi Paulo anali kulankhula kawiri-kawiri za Mtanda wa Yesu molunjika. Kodi n’chifukwa chiyani ichi chinali chonchi? Chifukwa ndi umboni omaliza wa chipulumutso chathu. Kukanakhala kuti Yesu anatenga machimo onse a dziko pa Iye yekha ndi kulephera kukhetsa mwazi pa Mtanda kuti alandire chiweruzo cifukwa cha ife, sitikanapulumutsidwa mwathunthu. Ichi ndi chifukwa chake Mtumwi Paulo analankhula za Mtanda kawiri-kawiri. Mtanda ndi ntchito yomaliza mu chipulumutso chathu.
Kukanakhala kuti choonadi cha chipulumutso chinaperekedwa kum’badwo uno popanda kulakwitsidwa, panthawi ino kukanakhala anthu ambiri opanda uchimo. Koma mwatsoka, choonadi chinataika kale-kale ndipo anthu ambiri akudziwa za Mtanda okha popanda kuzindikira tanthauzo leni-leni la ubatizo Wake.
Chifukwa ali ndi chikhulupiliro cha mchigoba chokha chopanda kathu cha uthenga wabwino, azakhalabe ochimwa ngakhale ndi zaka zingati angakhale ali kukhulupilira molimbika mwa Yesu. Azakhalabe ochimwa patapita zaka khumi, ngakhalenso patapita zaka makumi asanu a moyo wachipembedzo.
UMBONI WANGA
Kodi Mulungu amaona ochimwa ngati olungama?
Ai. Iye ndi wolungama. Wolungama ndi aja amene anamasulidwa kuuchimo, anapereka machimo awo onse pa Yesu kudzera mu ubatizo Wake.
Ndinayamba kukhulupilira mwa Yesu pamene Ndinali ndi zaka makumi awiri (20). Isanafike nthawiyo, sindinkadziwa kuti ndinachita machimo angati mu umoyo wanga chifukwa sindinkadziwa lamulo la Mulungu. Ndinali kuzikhalila m’njira yanga yanga popada kudziwa Mulungu kufika nthawiyo.
Kenako Ndinadwala. Ndinadwala kwambiri kotero kuti ndinali kuganiza kuti ndidzafa. Pachifukwa ichi, Ndinaganiza kuti Ndiyenera kuomboledwa kumachimo anga onse imfa yanga isanafike. Chifukwa Ndinamvapo kuti Yesu anafera ochimwa ngati ine, Ndinaganiza zokhulupilira mwa Iye. Pachiyambi, Ndinali odzaza kwambiri ndi chimwemwe ndi mathokozo. kwakuti ndinali kuti ndizafa. Ndiye, ndinati mwina ndiomboledwe kumachimo anga onse ndisanafe.
Koma kukondweraku kunayamba kutha pang’ono-pang’ono. Patapita zaka zochepa, sindinapewe koma kuchita machimo atsopano tsiku ndi tsiku. Ndinakhalanso ochimwa kawiri kawiri. Patapita zaka khumi, ndinali ochimwabe, makamaka oipitsitsa kuposa kale. Ndinakhulupilira mwa Yesu kwa zaka khumi, ndipo choona chakuti Ndinali ochimwa sichinasinthe. Ndinali okhulupilira ndiponso ochimwa.
Ngakhale kuti ndinkaimba, “♪Kulira sikudzandipulumutsa! Ngakhale nkhope yanga inasambitsidwa mu misozi, sikungachotse mantha anga, sikungatsuke uchimo wa zaka! Kulira sikudzandipulumutsa! ♪” Ndinali kulira nthawi iliyonse ndikachimwa.
“Okondedwa Mulungu, chonde Ndikhululukireni pa tchimo limodzili. Ndikhululukireni kamodzi kokha aka, ndipo sindidzachimwanso.” Ndikachimwa, ndinkapemphera kwa masiku atatu. Ndinali kuzitsekera m’chipinda chapangodya ndi kupemphera uku ndikusala kudya kwa masiku atatu. Chifukwa chikumbumtima changa chinali cholema kwambiri, Ndinalira ndi kupempha chikhululukiro cha Mulungu. Patsiku lachitatu, Ndinali kumvera bwino ndi kuganiza kuti ndingaloledwe pamaso pa Iye.
“Kachiwirinso, ndatsuka machimo anga. Aleluya!” Choncho, ndinatuluka ndi kukhala mosamala kwa kanthawi. Koma posachedwa ndinachimwanso ndipo kulakalaka kwanga kunakula. Ndinazowera kubwereza kukhala mwachisoni nthawi ndi nthawi. Chinali kumveka chokondweretsa kukhulupilira mwa Yesu pachiyambi, koma m’kukula kwa nthawi, m`mene ndinakhulupilira, ndi m’mene machimo anga anachulukirachulikira ngati fumbi m’chipinda chotsagwiritsidwa nchito.
Patatha zaka khumi, ndinakhala ochimwa oipitsitsa kupambana m`mene ndinayambira. “Kodi n’chifukwa chiyani ndinakhulupilira mwa Yesu mwamsanga? Chikanandipepukira kwambiri kukhulupilira mwa Yesu pamene ndafika zaka makumi asanu ndi atatu (80), ndisanafe. Kenako, sindikanazindikira za tchimo ndi kulapa tsiku ndi tsiku.” Ndinaganizira kuti ndikhale malingana ndi chifuniro cha Mulungu, koma zinali zosatheka. Ndinkaona ngati nditha kupenga!
Ndinayamba kumufuna-funa Mulungu mwatsopano. Ndinataya nthawi yaitali kuphunzira zamulungu. Koma patapita zaka zochepa, mtima wanga unakhala osakhutitsidwa ngakhalenso kwakukulu. Ndisanayambe kuwerenga mabuku a ziphunzitso za zipembezo, ndinazolowera kunanea kuti Ndikufuna kukhala ngati oyera mtima Damieni, kusagona pakama wotentha mwaufulu. Ndinalumbila kuti si ndidzazikondweretsa ndekha, m’malo mwake ndidzazipereka ndekha mwathunthu kuosowa.
Pamene Ndinali kuwerenga za moyo wa oyera mtimayu, ndinalumbila kukhala ngati iye. Ndinayesa kukhala moyo wodzichepetsa ndekha. Ndinazolowera kugwada pansi polimba ndi kupemphera kwa maola nthawi zina. Pachifukwa ichi, ndinali kumva ngati mapemphero anga anali ndi tanthauzo kwambiri ndipo Ndinali kumva bwino za ine ndeka pambuyo pake.
Koma patatha zaka khumi, ndinalepera kuipilira. Chotero ndinapemphera kwa Mulungu. “Okondedwa Mulungu Kumwamba, chonde ndipulumutseni. Ndikukhulupilira mwa Inu ndi mtima wanga wonse. Ndikudziwa kuti sindingasinthe kudzipereka kwanga kwa Inu ngakhale wina atandiika mpeni pankhosi panga. Koma ngakhale ndimakhulupilira mwa Inu ndi mtinga wanga wonse, kodi n’chifukwa chiyani ndimamvabe kuperewera mkati mwanga? Kodi n’chifukwa chiyani ndine osokonezeka kwambiri? Kodi n’chifukwa chiyani ndikukhala ochimwa kwambiri kuposa kale? Sindinaganizepo kwambiri za uchimo kuyambira kale. Ndinakhulupilira mwa Inu ndipo tsopano ndikudabwa chifukwa chimene ndakhalira oipitsitsa kwambiri pambuyo pakukhala ndi chikhulupiliro mwa Inu kwa zaka zambiri. Kodi bvuto ndi chiyani kwa ine?”
Panali pa nthawiyi, pamene ndinadziwa chifukwa chake. Ndinakhulupilira mwa Mulungu popanda kupulumutsidwa kumachimo anga. Sindinkadziwa choonadi panthawiyo, ndipo chinali chokwanira kundisokoneza.
Ndi uchimo mu mtima mwanga, kodi ndikanauza bwanji ena zachiombolo cha chisomo cha Mulungu? Kodi ndikanauza bwanji ena kuti akhulupilire mwa Yesu? Ndinapemphera mobwereza-bwereza. “Okondedwa Mulungu, posachedwapa ndidzamaliza maphunziro a pa seminale ndipo ndidzazozedwa ngati mtumiki. Koma ngati ndidzakhala mtumiki olema ndi uchimo, kodi ndidzauza bwanji ochimwa ena zakuomboledwa? Ndine wochimwa ine mwini ndipo ngati ndawerenga Makalata a mtumwi Paulo dinapeza kuti ngati wina alibe Mzimu wa Kristu, iye si mwana wa Mulungu. Koma ngakhale ndifune-fune motani, Mzimu suli mwa ine. Pachiyambi ndinali kumva ngati uli mwa ine, koma wandichokera. Kodi ndichiyani chinachitika? Chonde ndiuzeni chifukwa chake, Ambuye.”
Moona, chifukwa chinali chakuti ndinazinama ndekha poganiza kuti ndinaomboledwa kudzera mu chikhulupiliro chosavuta mwa Yesu. Ndinaganizirapo za izi kwa nthawi yaitali.
Mulungu analonjeza kuti adzazionetsa Iye yekha kwa aja amene amufunafuna kwambiri. Iye anakumana nane m’choonadi Chake pomaliza. Ndinali wochimwabe kwa zaka khumi pamene ndinayamba kukhulupilira mwa Yesu. Koma pamene ndinaphunzira zachisinsi cha ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, pamene ndinadziwa tanthauzo la mdulidwe mu Chipangano Chakale ndi mdulidwe wa uzimu mu Chipangano Chatsopano, pamene ndinazindikira ndi kukhulupilira m’chinsinsi cha chipulumutso kudzera mu ubatizo wa Kristu, mavuto anga onse anatha. Moyo wanga unayera mbuu ngati matalala.
Chidzakhala chimodzi-modzi kwa inu. Ngati mukhulupilira mu uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, inunso mudzakhala opanda chimo. Mungakhale operewera, koma mudzakhala wolungama. Mukatenga choonadi ichi m`mitima yanu ndi kudziwitsa izi kwa anthu ena, naonso adzapulumutsidwa ndi kuthokoza Mulungu, kufuura “Aleluya!”
Ndikufuna kuyamikira abale onse ndi alongo amene anaomboledwa. Ndikutamanda Yesu potipulumutsa kumachimo athu onse. Aleluya! Tinaomboledwa mosangalala kumachimo athu onse.
Ndidalitso lalikulu kotero kuti sititha kuonetsa chisangalalo chathu chonse ndi mawu. Tiyeni tiimbe nyimbo pamodzi. “♪Zina lake lakhala chinsinsi, poti sitinalengezebe zinsinsi kuzolengedwe zonse. Iye anaponyedwa kunja ngati miyala anaikana amisiri, koma dzina Lake linakhala miyala yonyezimila yamtengo wapatali mumtima wanga♪”.
UBATIZO WA YESU NDI MWAZI WAKE NDI OKWANIRA KWAMBIRI KUPULUMUTSA OCHIMWA ONSE KUMACHIMO AWO
Kodi n’chiyani chimachotsa machimo onse kumitima yathu?
Ubatizo wa Yesu
Yesu Kristu anachotsa machimo onse adziko kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi. Iye anatidula mu uzimu ndi kutipanga anthu Ake. Iye ndi Mulungu wa obadwa mwatsopano.
Masiku onse kuli chiweruzo cha uchimo. Koma Yesu anabatizidwa ndi kuweruzidwa pa Mtanda kuti atipulumutse. Ndi mwazi Wake, Iye anatipulumutsa tonse ndipo Iye anaukitsidwa patsiku lachitatu. Anali Atate Mulungu amene anautsa Yesu ku akufa.
Moyo wa Yesu ndi moyo wathu ndi chizindikiro cha kukhalapo kwathu ngati ana a Mulungu. Ubatizo Wake unachotsa machimo athu onse ndipo mwazi wamtengo wapatali wa Yesu pa Mtanda ndi umboni wakuti Iye analandira chiweruzo m’malo mwathu.
Okondedwa abwenzi, kodi muli nawo umboniwu wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake m`mitima yanu? Ndikukufunsaninso. Kodi chipulumutso chathu chinabwera kudzera mu mwazi wa Yesu okha? Ai, chimabwera kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi mu mwazi Wake pamodzi.
KODI NDI NDANI WAMPATUKO?
Kodi ndi ndani wampatuko?
Iye ndi amene amadziweruza yekha mwa kulemphera kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu
Okondedwa abwenzi, kodi ndinu ochimwabe posawerengera kuvomereza kwa chikhulupiliro chanu mwa Yesu tsiku lililonse la moyo wanu? Ngati ndinu ochimwa ngakhale kuti mukukhulupilira mwa Yesu, ndiye kuti ndinu ampatuko. Mpatuko ndi kusakhulupilira mu choonadi cha Mulungu. Tito 3:10-11 akulankhula za mpatuko, “Munthu wopatukira cikhulupiriro, atamcenjeza kamodzi ndi kawiri, amkanize podziwa kuti wotereyo wasandulika konse, nacimwa, nakhala wodzitsutsa yekha.”
Monga munthu odzitsutsa yekha akuti, “Okondedwa Mulungu! Ndine ochimwa. Ndimakhulupilira mwa Inu, koma ndine ochimwabe. Palibe kanthu chimene munthu aliyense anganene, Ndine ochimwa ndipo ndikudziwa kuti izi ndi zoonadi.”
Mulungu akunena kwa iye, “kodi iwe ndi ochimwabe ndipo si ndiwe mwana wa Ine? Tsono, ndiwe wampatuko, ndipo udzaponyedwa mu moto wa gehena.”
Ngati m’makhulupilira mwa Yesu popanda kukhulupilira mu uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu mu mtima mwanu, ngati mukudziweruza nokha ngati ochimwa ndi kuvomereza kwa Mulungu kuti mzimu wanu uli ndi uchimo, ndiye kuti ndinu wampatuko pamaso pa Mulungu.
KODI OKHULUPILIRA OONA NDI NDANI?
Kodi umboni wa Mulungu wa chipulumutso ndi chiyani?
Madzi, mwazi, ndi Mzimu
Onse aja amene amakhulupilira mu uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, Onse aja amene anakhala anthu a Mulungu, ndi onse aja amene machimo awo anachotsedwa ndi olungama. Kodi mungakhale ochimwa bwanji pamene mukhulupilira mwa Yesu? Ochimwa sangalowe mu Ufumu wa Mulungu.
Onse aja akukhala olungama mwa kukhulupilira mwa Yesu ali ndi umboni wa Mulungu m’mitima yawo. Umboni ndi ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Nchito yachipulumutsoyi ndi imene Yesu Kristu anachita padzikoli.
Pacifukwa ichi, wina aliyense amene akukana kukhulupilira mu uthenga wabwino wa ubatizo umene Yesu anachotsera machimo athu onse adzadulidwa kwa Mulungu.
Okondedwa abale ndi alongo mu chikhulupiliro, kodi mukubvomera m’mitima yanu uthenga wabwino kuti chipulumutso cha ochimwa si mwazi wa Yesu okha, koma ndi madzinso amene ndi ubatizo wa Yesu?
Aliyense amene akhulupilira mu ntchito imene Yesu anachita m’dzikoli, ndipo aliyense amene abvomera madzi, mwazi, ndi Mzimu, adzapulumutsidwa ku uchimo wake onse. Ichi ndi choonadi ndipo ndi nzeru ya uthenga wabwino wa madzi, mwazi, ndi Mzimu.
Yesu anatitsuka mwathunthu ku uchimo wathu onse kudzera mu ubatizo Wake kuti anthu onse apulumutsidwe kudzera mwa Iye. Tsopano, ngati mukukhulupiliradi mwa Yesu, palibe njira ya inu yokhalira ochimwa.
Yesu anatiukitsa ife kwa akufa. Iye anapulumutsa miyoyo yonse imene inachoka kwa Mulungu chifukwa cha chinyengo cha Mdielekezi. Yesu akufuna kupeza miyoyo yonse yotaika. Mulungu wagwira ntchito kudzera mwa Yesu mwa uthenga wabwino wa madzi, mwazi ndi Mzimu. Iye anatiitana ndipo tsopano tingaomboledwe ndikupulumutsidwa ndi Iye.
Kodi mukukhulupilira mu choondi ichi chakuya? Ndikukuuzani kuti chipulumutso sichili mu mwazi okha, koma mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda. Onse aja amene akuti anapulumutsidwa mwa mwazi okha ayenera kuzindikira kuti ali ndi uchimo m’mitima yawo.
Tonse tinazolowera kuganiza kuti kunali kokwanila kwa chipulumutso chathu kukhulupilira mu mwazi a Yesu. Tinali kuganiza choncho poyamba, koma tsopano tiyenera kuzindikira kuti sikokwanira. Tinapulumutsidwa ndi kubadwa mwatsopano mwa kukhulupilira mwa Yesu Kristu, amene anabwera mwa madzi, mwazi, ndi Mzimu.
Ochimwa aliyense angabadwe mwatsopano kudzera mu chikhulupiliro mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake (1 Yohane 5:5-10). Tiyeni Tithokoze Mulungu. Aleluya!