(Aroma 8:28-30)“Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwacitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wace. Cifukwa kuti iwo amene Iye anawadziwiratu, iwowa anawalamuliratu afanizidwe ndi cifaniziro ca mwana wace, kuti Iye akakhale mwana woyamba wa abale ambiri; ndipo amene Iye anawalamuliratu, iwo anawaitananso; ndimo iwo amene Iye anawaitana, iwowa anawayesanso olungama; ndi iwo amene Iye anawayesa olungama, iwowa anawapatsanso ulemerero. ”
Kodi Mulungu anasankhadi ena a ife okha moona?
Ai. Iye anasankha ife tonse mwa Yesu Kristu.
Maphunziro a Chiphunzitso a kukonzedweratu ndi chisankho cha Umulungu, chimene ndi chimodzi mwa maphunziro aakulu amene akupanga chiphunzitso cha Chikristu, chapangitsa ambiri amene akufuna kukhulupilira mwa Yesu kuti asadziwe bwino mawu a Mulungu. Phunziro losocheretsali lapangitsa msokonezo waukulu.
Chimene maphunziro abodza akunena za kukonzedweratu ndi chakuti Mulungu anasankha anthu amene Iye anakonda pamene iwo amene sanawakonde akuwaweruza. Izi zikutanthauza kuti ena amene anasankhidwa ndi obadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu ndipo ndiololedwa Kumwamba pamene ena amene sanasankhidwe ndi oyenera kutenthedwa ku gahena.
Ngati ndi zoonadi kuti Mulungu wasankha ena a ife okha, sitingathandize koma kuda nkhawa pa funso lakuti, “Kodi ndinasankhidwa kuchipulumutso?” Ngati sitinasankhidwe, kukanakhala kopanda ntchito kwa ife kukhulupilira mwa Yesu. Motero phunziro limeneli lapanga anthu ambiri kuda nkhawa kuti mwina anasankhidwa ndi Mulungu koposa chikhulupiliro chenichenicho.
Ngati tikhulupilira zimenechi kodi tingamasuke bwanji ku chikaiko ndi kukhulupilira mwa Mulungu yekha? Kodi tingatsimikize bwanji kuti Mulungu zoonadi anatisankha ife? Iye adzakhala Mulungu wa okhao amene anawasankha, ngakhale akunena kuti, “Kapena Mulungu ndiye wa Ayuda okha okha kodi? Si wao wa amitundunso kodi? Eya, wa amitundunso” (Aroma 3:29).
Chifukwa anthu ambiri samvetsetsa tanthauzo la kukonzedweratu ndiponso chisankho cha Umulungu, akuopa kuti adzaonongedwa ngakhale kuti amakhulupilira mwa Yesu.
Aefeso 1:3-5 akunena kuti, “Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m’zakumwamba mwa Kristu; monga anatisankha ife mwa Iye, lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda cirema pamaso pace m’cikondi. Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana a Iye yekha mwa Yesu Kristu, monga umo kunakomera cifuniro cace.”
Motero tiyenera kuonanso lingaliro la phunziro la kukonzedweratu ndi chisankho cha Umulungu. Tiyenera choyamba kuzindikira zimene Baibulo likunena za kukonzedweratu ndi chisankho cha Umulungu ndi kulimbitsa chikhulupiliro chathu mu chipulumutso kudzera mu madzi ndi Mzimu.
Kodi Aroma akutiuza chiani? Azipembezo ena amakhala ndi phunzitso lopanda pake la “chisankho chopanda malire.” Ndiyeno, kodi chipembedzo ndi Mulungu? Chipembedzo chokha si Mulungu.
Ngakhale pamene dziko lisanalengedwe, Mulungu anasankha mtundu wa anthu onse mwa Yesu Kristu ndipo anaika maganizo Ake kuti apulumutse ife tonse mwa kutipanga ife kukhala olungama. Yesu amatikonda mopanda malire. Osamupanga Iye kukhala Mulungu wachisankho. Osakhulupilira ali ndi chikhulupiliro cha m’maganizo mwawo koma okhulupilira amaika chikhulupiliro chawo chonse mu mawo olembedwa a Mulungu.
CHISANKHO CHA UMULUNGU MU CHIPANGANO CHAKALE
Kodi chiphunzitso cha chisankho chopanda malire ndi choona?
Ai. Ambuye wathu si Mulungu wa maganizo-ochepa. Mulungu anasankha ochimwa onse mwa Yesu, osati osankhidwa ochepa okha.
Mu Genesis 25:21-26, timawerenga za ana awiri a Isake, Esau ndi Yakobo. Mulungu anasankha Yakobo pamene ana onse awiri a Isake anali m’mimba mwa amai awo.
Iwo amene samvetsetsa mawu a Mulungu amatenga chimenechi ngati chiyambi cha phunziro la chisankho chopanda malire. Izi zili monga kusakaniza mulungu olosera mu Chikristu.
Ngati tikhulupilira kuti Mulungu anasankha ife pa chifukwa cha “chisankho chopanda malire” ndipo osati mwa Yesu Khristu, ndiye kuti ndi chimodzimodzi kuti tikulambira mulungu olosera ndi mafano. Mulungu simulungu olosera. tikanati tikhulupilire mwa mulungu olosera, tikanakana chikonzero cha Mulungu pa ife ndi kugwera mu msampha wa Satana.
Ngati anthu samvera chifuniro cha Mulungu, ndiye kuti ali chabe ngati chirombo chimene chili choyenera kuonongedwa. Popeza ife okhulupilira sindife zilombo, tiyenera kukhala okhulupilira oona amene timawerenga ndi kukhulupilira mu choonadi cholembedwa mu Baibulo. Kupanda kuganiza poyamba za choonadi cholembedwa Mbaibulo ndi kuzipereka tokha kwa Satana.
Kuti tikhale ndi chikhulupiliro choona, tiyenera choyamba kuganiza za choonadi cholembedwa Mbaibulo ndi kutsatira chikhulupiliro cha iwo obadwanso mwa Kristu.
Ziphunzitso za kavini zinakakamira pa chiombolo cha malire. Ichi chikusonyeza kuti chikondi cha Mulungu ndi chiombolo cha Ambuye sichili pa ena. Kodi izi zingakhale zoona?
Baibulo limanena kuti, “Mulungu mpulumutsi wathu; amene akufuna anthu onse apulumuke” (1 Timoteo 2:4). Ngati dalitso la chiombolo lili pa ochepa okha, okhulupilira ambiri akanasiya kukhulupilira mwa Yesu. Kuphatikizo apo, ndani angafune kukhulupilira mwa Mulungu waganizo-lochepa?
Tiyenera kukhala ndi chilimbikitso kuti Mulungu wathu si Mulungu ali ndi ganizo-lochepa. Iye ndi Mulungu wa Choonadi, wa Chikondi, ndiponso wa Chilungamo. Tiyenera kukhulupilira mwa Yesu ndi uthenga wabwino wa kubadwa mwatsopano wa madzi ndi Mzimu ndipo motero tikhale opulumutsidwa ku machimo athu onse. Yesu ndi Mpulumutsi wa onse amene ndi obadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.
Kulingana ndi chiphunzitso cha Kavini, ngati pali anthu khumi, ena a iwo angapulumutsidwe ndi Mulungu pamene ena angasiyidwe kuti akatenthedwe mu moto wa kugehena. Izi sizoona.
Zilibe nzeru kunena kuti Mulungu amakonda ena ndi kudana ndi ena. Taganizani kuti Mulungu alipano pamodzi nafe lero. Ngati angaganize zosankha iwo amene akhala kuzanja lamanja ndi kupanga ganizo Lake kuti apereke onse amene akukhala kuzanja lamanzere ku gehena, kodi tingamuone ngati Mulungu?
Kodi iwo amene azasiidwa sazachotsa mawu awo mwa zionetsero? Zolengedwa zonse zingalire, “Kodi Mulungu angakhale bwanji chonchi wopanda chilungamo?” Chisankho chopanda malire ndi chabodza chifukwa Mulungu anasankha mtundu onse wa anthu mwa Yesu Kristu.
Motero aliyense amene akuitanidwa ndi Mulungu m’dzina la Kristu anasankhidwa. Ndiyeno, kodi ndani amene Mulungu akumuitanira kwa Iye? Iye amaitana ochimwa, osati olungama. Mulungu samaitana iwo amene akuziona ngati ndi olungama.
Dalitso la Mulungu la chiombolo ndi la ochimwa ndiponso iwo amene ali owonongedwa ku gehena. Chisankho chikutanthauza kuti Mulungu aitana ochimwa kuti awapange kukhala ana Ake olunguma.
MULUNGU NDI WOLUNGAMA
Kodi Mulungu amakonda osankhidwa ochepa okha?
Ai, Ambuye Sali ochepa-nzeru. Mulungu ndi wolungama.
Mulungu ndi wolungama. Iye si Mulungu amene wakonda osankhidwa okha opanda malire. Iye amaitana ochimwa mu dzina la Kristu. Popanda chipulumutso kudzera mu chiombolo cha Yesu Kristu ndi chikhululukiro cha machimo, kodi tikanadziwa bwanji chikondi cha Mulungu ndi chipulumutso? Osapanga Iye kukhala Mulungu opanda chilungamo.
Yesani kupeza chimene chikusowa pamene mukuwerenga Aefeso 1:3-5. “Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m’zakumwamba mwa Kristu; monga anatisankha ife mwa Iye, lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda cirema pamaso pace m’cikondi. Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana a Iye yekha mwa Yesu Kristu, monga umo kunakomera cifuniro cace.” Kodi chikusowa ndi chiani? Mawu amene akusowa ndi akuti “mwa Yesu Kristu.”
Chisankho chopanda malire mu chiphunzitso cha Kavini sichigwirizana ndi mawu a Mbaibulo. Baibulo limanena kuti, “monga anatisankha ife mwa Iye, lisanakhazikike dziko lapansi”
Mulungu anasankha mtundu wa anthu onse mwa Yesu kuti abadwe mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Iwo amene sangadzithandize koma kubadwa ochimwa angaomboledwe ku uchimo ndi kukhala ana Ake. Anaphatikizapo mtundu onse wa anthu mu m’ndandanda wa iwo amene adzapulumutsidwa ndi kuwasankha iwo mwa Yesu Kristu.
Chifukwa azaumulungu ambiri amene akukakamira pa chisankho chopanda malire amanena kuti ochepa okha ndi amene ali osankhidwa, anthu ambiri ndi ogwidwa mu zowawa za kukhulupilira mu ziphunzitso zosaganizidwa bwino. Azipembezo onyengawa amanena kuti Mulungu amasankha ochepa ndi kusiya ena kudzera mu chisankho chopanda malire, pamene choonadi cha mawu Ake ndi chakuti Mulungu anasankha ochimwa onse mwa Yesu. Anthu ambiri amagwidwa mu ziphunzitso zabodza zokhudzana ndi zikhulupiliro zawo zosaganiza bwino.
Zindikirani chimenecho ndipo ngati muzazindikira kuti Mulungu anaganiza zopulumutsa mtundu wa a anthu mwa Yesu, ndiponso kuti chikhululukiro cha uchimo chili pa aliyense amene akhulupilira mwa Yesu. Mwa kutero, tingapulumutsidwe ku machimo athu onse, kukhala ana a Mulungu, kukhala ndi moyo osatha, ndi kukhala ndi chilimbikitso kuti Mulungu ndiye chilungamo.
CHISANKHO CHA UMULUNGU MU NKHANI YA YAKOBO NDI ESAU
Kodi Mulungu anasankha ndani? Kodi ndi Osankhidwa okha?
Ai.Mulungu anasankha mtundu onse wa anthu mwa Kristu.Choncho, aliyense amene akhulupilira mwa Kristu ndipo alibe tchimo kudzera mu ubatizo wa Yesu ali osankhidwa.
Mu Genesis 25:19-28, Esau ndi Yakobo anali kuvutikira pamodzi mkati mwa mimba ya amai awo Rabeka. Mulungu ananena kuti mu 25:23, “Yehova ndipo anati kwa iye, Mitundu iwiri iri m’mimba mwako, magulu awiri a anthu adzaturuka m’mimba mwako; gulu lina lidzapambana mphamvu ndi linzace; wamkuru adzakhala kapolo wa wamng’ono.’”
Ochimwa amatembenuza mawu amenewa kukhala phunziro la maphunziro a kukonzedweratu ndi chisankho cha Umulungu, kusiya ambiri amene akhulupilira mwa Yesu ali okaikira kuti mwina ali osankhidwa kapena ai! Ngati aziona okha kukhala osankhidwa, amaganiza kuti apulumutsidwa ndi kuleka kuikira nzeru mu kukhala obadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.
lingaliro la chisankho chopanda malire lasintha anthu ambiri amene akhulupilira mwa Yesu kutalikirana ndi chiombolo ndi kuwaweruzira iwo ku gehena. Ndipo chaonetsanso Mulungu kukhala osalungama.
Chifukwa azipembedzo ambiri amaphunzitsa chiphunzitso chabodza chimene chikuphukira mu maganizo awo, ambiri amene akhulupilira mwa Yesu amakhala osatetezeka ndipo amada nkhawa ngati anasankhidwa, kapena mwina chiombolo chawo chinali chosankhidwa.
Pa Yakobo ndi Esau, kodi ndani yemwe Mulungu anasankha? Anasankha Yakobo mwa Yesu Kristu. Mu Aroma 9:10-11, akunena kuti Mulungu anaitana Yakobo m’malo mwa m’bale wake ngakhale kuti anabadwa kwa munthu m’modzi, ngakhale asanabadwe, ndiponso sanachite kanthu kalikonse koipa kapena kabwino.
Cholinga cha Mulungu chinali cha kusankha Yakobo, osati chifukwa cha ntchito zake koma chifukwa cha chisankho Chake. Baibulo likutiuzanso kuti Yesu anabwera kuzaitana ochimwa, osati iwo amene akhala moyo woongoka.
Anthu onse, monga m’badwo wa Adamu, anabadwa ali ochimwa. Davide ananena kuti anali ochimwa kuchokera panthawi imene anali m’mimba mwa amai ake ndi kuti anabadwira mu zolakwa. “Onani, ndidabadwa m’phulupulu: Ndipo mai wanga anandilandira m’zoipa” (Masalimo 51:5).
Anthu onse amabadwa ochimwa chifukwa cha machimo ya makolo awo. Choncho aliyense amene ndi obadwira m’dzikoli mosadziwa amakhala ochimwa, amachita monga ochimwa ndipo amabala zipatso za uchimo.
Mwana amene sanachitepo chimo lililonse ali kale ochimwa chifukwa anabadwa kuchokera ku mbewu ya uchimo. Iye ali ndi maganizo oipa, chigololo, chiwerewere ndi kupha mu mtima wake. Iye anabadwa ndi machimo a makolo ake. Anthu onse ndi ochimwa ngakhale asanabadwe.
Chifukwa chimene Mulungu anatipangira wodwala ndi chakuti. Mtundu wa anthu ndi chilengedwe cha Mulungu, koma Ambuye anali ndi chikonzero chotipanga kukhala ana Ake mwa kutipulumutsa ku uchimo. Ndi chifukwa chake Iye analola Adamu kuchimwa.
Pamene takhala ochimwa zotsatira zake, Mulungu anatuma Yesu ku dzikoli, kulola Mwana Wake obadwa yekha kuti achotse machimo onse a mtundu wa anthu kudzera mu ubatizo Wake.
Cholinga cha Mulungu ndi kuombola mtundu wa anthu kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda ndi kuwapatsa mphamvu yokhala ana Ake mwa kukhulupilira mwa Yesu. Iye analola Adamu kuchimwa pa lonjezo lakutsuka machimo onse mwa Kristu.
Ochimwa amene akhulupilira mu chiphunzitso chabodza amanena kuti, “Taonani Yakobo ndi Esau. Iye anasankha m’modzi ndi kusiya winayo popanda malire.” Mulungu sanasankhe ife popanda malire, koma anatisankha ife mwa Yesu Kristu. Tiyenera kungoyang’ana ku mawu olembedwa mu Baibulo. Aroma 9:10-12 anena kuti, “Ndipo si cotero cokha, koma Rabekanso, pamene anali ndi pakati pa mmodzi, ndiye kholo lathu Isake; pakuti anawo asanabadwe, kapena asanacite kanthu kabwino kapena koipa, kuti kutsimiza mtima kwa Mulungu monga mwa kusankha kukhale, si cifukwa ca nchito ai, koma cifukwa ca wakuitanayo, cotero kunanenedwa kwa uyo, wamkuru adzakhala kapolo wa wamng’ono.’”
Mulungu anasankha Yakobo mwa Yesu. Yakobo anali chionetsero cha ochimwa amene anali osayenera ndiponso osiyidwa ku chilungamo chawo. Aefeso 1:4 anena kuti Mulungu anasankha ife mwa iwo.
Kodi Mulungu anaitana ndani? Iye anaitana Yakobo chifukwa Yakobo anadziwa kuti anali ochimwa ndiponso osalungama pamaso pa Mulungu ndipo ankadalira mwa Mulungu. Iye anaitana Yakobo mwa dzina la Mwana Wake Yesu ndipo anamuombola ndi uthenga wabwino wa madzi ndi mwazi kuti amupange kukhala mwana Wake. Choncho, Mulungu anaiyana Yakobo ndi kumudalitsa ndi chiombolo.
Iye anaitana ochimwa kuti awapamge akhale olungama kudzera mu chiombolo cha Yesu. Icho chinali chikonzero cha Mulungu.
CHIPHUNZITSO CHABODZA CHA CHISANKHO CHOPANDA MALIRE
Kodi n’chifukwa chiani Mulungu anakonda Yakobo?
Chifukwa chakuti Yakobo anadziwa kusalungama kwake.
Posachedwapa ndinawerenga buku lonena za nkhani ya chisankho chopanda malire. Munthu wachichepere anali ndi loto. Mayi wachikulire anaonekera ku maloto ndi kuuza wachichepereyo kuti abwere ku malo ena, ndipo iye anapita. Ndiyeno mayi wachikulireyo anamuuza kuti anasankhidwa ndi Mulungu.
Iye anafunsa mayi wachikulireyo kuti zingatheke bwanji Mulungu kumusankha iye pamene sanali kukhulupilira ndi pang’ono pomwe mwa Mulungu? Iye anamuuza kuti Mulungu anasankha iye mopanda malire ngakhale kuti sanali okhulupilira.
Izi sizoona. Kodi Mulungu angaweruze bwanji anthu mwaufulu ndi kupita nawo ku gehena ndiponso kusankha ena kupita ku chipulumutso? Mulungu anasankha aliyense mwa Yesu.
Chiphunzitso cha chisankho chimene chimapatula Yesu ndi chabodza. Ndi chonama. Koma ophunzitsa zaumulungu ambiri amakakamira kuti Mulungu anasankha ena a ife okha. Izo ndi zabodza. Mulungu akufuna kupulumutsa aliyense mwa Yesu. Okhawo amene sakhulupilira mu chiombolo cha madzi ndi Mzimu mwa Yesu ndi amene sadzapulumutsidwa.
Mulungu anakonzeratu mtundu onse wa anthu ku chipulumutso kudzera mwa Mwana Wake, Yesu, ndipo anafunanso kupanga ife kukhala ana Ake ngakhale pamene dziko lapansi lisanapangidwe. Iye anakonzeratu kuti apulumutse mtundu wa anthu ku machimo onse a dziko lapansi kudzera mu chiombolo cha Yesu Kristu. Ichi ndi choonadi monga analembera mu Baibulo.
Olungama amene anabadwanso mwa Yesu Kristu ndi osankhidwa. Koma ophunzitsa zaumulungu amakakamira kuti Mulungu anasankha ena a ife okha. Iwo amanena kuti, mwachitsanzo, kuti mamonke a chibuda ndi amodzi amene Mulungu sanawasankhe. Koma Mulungu anasankhanso iwo mwa Yesu.
Ngati Mulungu anasankha ena mopanda malire, popanda Yesu, sitiyenera kulalikira uthenga wabwino. Ngati Mulungu anakonza kuti asankhe wina popanda Yesu, ochimwa sayenera kukhulupilira mwa Yesu. Kodi ndiyeno mawu Ake a chikondi, choonadi, ndiponso chiombolo akanakwaniritsidwa motani?
Kodi pakanakhala chifukwa chilichonse kwa atumiki a Mulungu kuti alalikire uthenga wabwino m’dzikoli? Kodi pali nzeru iliyonse kuti Mulungu anasankha kale owomboledwa ndi owonongedwa mopanda malire popanda Yesu?
Chifukwa chimene Mulungu anasankhira Yakobo mwa Yesu, chifukwa chimene Iye anakondera Yakobo ndi kudana ndi Esau ndi chakuti Iye anadziwiratu asanalengedwe kuti Yakobo adzakhulupilira mwa Yesu ndipo Esau sadzakhulupilira mwa Iye.
Muli ochimwa ambiri m’dzikoli amene amakhulupilira mwa Yesu. Ena a iwo ali ngati Esau ndipo ena ali ngati Yakobo.
Kodi n’chifukwa chiani Mulungu anakonda Yakobo? Yakobo anali osalungama ndipo ankadziwa za kusayenera kwake. Motero iye anavomereza kuti anali ochimwa pamaso pa Mulungu ndipo anapempha chisomo Chake. Ndi chifukwa chake Mulungu anapulumutsa Yakobo.
Koma Esau anadalira kwambiri pa yekha koposa Ambuye ndipo sanamvere njala ya chisomo cha Mulungu. Choncho Mulungu ananena kuti Iye akonda Yakobo ndi kudana ndi Esau. Awa ndi mawu a choonadi.
Mulungu anasankhiratu ife tonse ku chipulumutso mwa Yesu. Ochimwa onse chimene ayenera kuchita ndi kukhulupilira mwa Yesu. Ndiyeno Choonadi cha Mulungu ndi chilungamo chidzakhala m’mitima yawo. Ife ochimwa sitingachite kanthu koma kukhulupilira ndi mitima yathu yonse mu kupulumutsidwa kudzera mwa Yesu. Chimene tiyenera kuchita ndi kukhulupilira mu chiombolo kudzera mwa Yesu.
CHIPHUNZITSO CHONYENGA CHA CHIYERETSO MWA PANG’ONO PANG’ONO
Kodi ndi zoona kuti ochimwa angakhale olungama pang’ono pang’ono?
Ai. Ndizosatheka. Kamodzi kokha, Mulungu anapanga ochimwa kukhala olungama ndiponso opanda chilema kudzera mu chiombolo cha ubatizo Wake ndi imfa Yake pa Mtanda.
Satana akunyenga ochimwa ndi chiphunzitso cha chiyeretso mwa pang’ono pang’ono kotero kuti asapulumutsidwe ku machimo awo. Chiyeretso cha pang’ono pang’ono chikutanthauza kuti ochimwa pang’ono pang’ono amakhala oyera ngati akhulupilira mwa Yesu.
Nkhaniyi ikuyenda motere. Ochimwa sangakhale olungama kamodzi kokha koma amapulumutsidwa kokha ku uchimo weniweni pamene akhulupilira mwa Yesu. Machimo enieni amatsukidwa kudzera mu mapemphero a kulapa a masiku onse ndipo anthu pang’ono pang’ono amakhala akuyeretsedwa.
Mutu wa chiphunzitsochi ndi chiyeretso mwa pang’ono pang’ono. Chikumveka chabwino kuti wina angakhulupilire mwa Yesu ndipo pang’onopang’ono angakhale Mkristu oyera. Chiphunzitsochi chasocheretsa Akristu ambiri zaka zonsezi, kuwapanga iwo kukhala otetezeka. Icho ndi chifukwa chake kuli Akristu ambiri akuti-ndi oyera-koposa-kuyera kwa ena mu Chikristu.
Iwo amaganiza kuti tsiku lina adzasintha ndipo sadzachimwanso. Koma amakhala moyo wawo ngati ochimwa ndipo adzaweruzidwa ngati ochimwa pamaso pa Mulungu pambuyo pa imfa yawo.
Werengani mawu oona mu Baibulo. Mu Aroma 8:30, “Ndipo amene Iye anawalamuliratu, iwo anawaitananso; ndimo iwo amene Iye anawaitana, iwowa anawayesanso olungama; ndi iwo amene Iye anawayesa olungama, iwowa anawapatsanso ulemerero.”
Ndipo mu ndime ya 29, “Cifukwa kuti iwo amene Iye anawadziwiratu, iwowa anawalamuliratu afanizidwe ndi cifaniziro ca Mwana wace, kuti Iye akakhale mwana woyamba wa abale ambiri.” Tikaona poyamba pakuoneka ngati pali mapazi oyenera kukhala olungama. Koma Mawu akutiuza kuti chilungamo chinaperekedwa kamodzi kokha.
“Iwo amene Iye anawaitana, iwowa anawayesanso olungama.” Yesu anaitana ochimwa ndipo anawapanga iwo kukhala olungama kudzera mu ubatizo Wake pa Yordano ndiponso imfa Yake pa Mtanda.
Motero iye amene wakhulupilira mu chiombolo mwa Yesu amakhala mwana wa Mulungu mwaulemelero. Ndi chisomo cha Mulungu kuombolo ochimwa ndi kuwapatsa ulemelero m’dzina Lake.
Izi ndi zimene Mulungu akutiuza ife. Koma Akristu ena amatiuza ife kuti tione pa Aroma 8:30. “Pali mapazi kuti tikhale oyeretsedwa. Kodi izi Sizikutanthauza kuti tiyenera kusintha pang’ono pang’ono?” Umu ndi m’mene akunyengedwera. Iwo amauza anthu mu mthawi ya mtsogolo kuti ochimwa adzakhala olungama m’kupita kwa nthawi.
Koma Baibulo limatiuza ife osati mu mthawi ya mtsogolo, koma mthawi yakale kuti tinakhala olungama kamodzi kokha. Pali kusiyana koonekeratu pakati pa lingaliro la mtsogolo ndi lakale.
Tiyenera kukhulupilira mwanthunthu mu Baibulo. Kulingana ndi zimene zinalembedwa, tingakhale ana a Mulungu kamodzi kokha. Ichi ndi chosiyana kwambiri ndi chiphunzitso cha chiyeretso mwa pang’ono pang’ono.
Chiphunzitso cha chiyeretso cha pang’ono pang’ono chimanena kuti tchimo loyamba lokha ndi limene limakhululukidwa pamene takhulupilira mwa Yesu. Ichi chikuonetsa kuti tikuyenera kukhala ndi moyo wachipembezo ndi kulapa machimo athu masiku onse, kotero kuti pamene taima pamaso pa Mulungu, tizakhala olungama.
Chifukwa anthu ambiri amakhulupilira mu chiphunzitsochi, iwo amakhalabe ochimwa, ngakhale anayamba kukhulupilira mwa Yesu. Ndi chifukwa chake chiphunzitso cha chiyeretso mwa pang’ono pang’ono ndi chabodza.
Baibulo limatiuza poyera kuti timakhala olungama ndiponso ana a Mulungu mwa chikhulupiliro. Monga m’mene ana amabwerera kudziko, ana a Mulungu naonso amakhala oyeretsedwa pamene azindikira ndi kukhulupilira mu chiombolo cha Yesu. Chiphunzitso chonyenga cha chiyeretso mwa pang’ono pang’ono chikuchokera ku mabodza.
KUOMBOLEDWA KWATHUNTHU KU MACHIMO ONSE
Kodi tiyenera kuchita chiani kuti tiyeretsedwe kwathunthu?
Tiyenera kukhulupilira mu chiombolo cha madzi ndi Mzimu.
Aroma 8:1-2 anena kuti “Cifukwa cace tsopano iwo akukhala mwa Kristu Yesu alibe kutsutsidwa. Pakuti cilamulo ca mzimu wa moyo mwa Kristu Yesu candimasula ine ku lamulo la ucimo ndi la imfa.” Ichi chikutiuza kuti Mulungu anapanga ochimwa onse kukhala olungama ndi kuombola onse amene anabwera kwa Yesu kuchokera ku lamulo lauchimo ndi imfa.
Baibulo limatiuza za chiombolo chanthunthu mu Ahebri 9:12. “Kapena mwa mwazi wa mbuzi ndi ana a ng’ombe, koma mwa mwazi wa Iye yekha, analowa kamodzi ku malo opatulika, atalandirapo ciombolo cosatha.” Ichi chikutanthauza kuti ife amene tikukhulupilira mwa Yesu ndife woomboledwa ndipo tikuvomerezedwa Kumwamba.
Tinamva ndi kukhulupilira uthenga wabwino wa chiombolo mwa madzi ndi Mzimu mwa Yesu Kristu ndipo tinakhululukidwa ku machimo athu onse. Koma ochimwa amene akhulupilira kuti amakhululukidwa ku tchimo lobadwa nalo lokha sangapulumutsidwe moonadi. Kuti ayeretsedwe ku machimo amene amachita pamene akhulupilira mwa Yesu, amazimva kuti ayenera kulapa masiku onse.
Chikhulupiliro chawo chosalondola chikuwatsogolera ku gehena. Zikhulupiliro zawo zolakwikwa ziwapangitsa kulapa masiku onse kotero kuti amasuke okha ku mphulupulu zawo zonse. Icho sichikhulupiliro choona chimene chingatipulumutse ku gehena.
Akanakha kuti anakhulupilira mwa Yesu ndipo anaomboledwa kamodzi kokha, akanakhala olungama ndiponso ana a Mulungu. Chiombolo Choona chimapangitsa okhulupilira kukhala olungama ndikuwasintha kukhala ana a Mulungu kamodzi kokha.
Ngakhale kuti okhulupilira aomboledwe ku machimo onse a dziko, thupi lawo silimasintha kufikira tsiku limene adzafe. Koma mitima yawo imanyowa ndi chilungamo cha Mulungu. Sitiyenera kuzindikira molakwika choona chimenechi.
Baibulo limatiuza kuti timayeretsedwa ndi kukhala olungama pamene takhulupilira mu uthenga wabwino.
Tiyeni tione pa Ahebri 10:9-14 kuti tione uthenga wabwino oona. “Pamenepo anati, Taonani, ndafika kudzacita cifuniro canu. Acotsa coyambaco, kuti akaike caciwirico. Ndi cifuniro cimeneco tayeretsedwa mwa copereka ca thupi la Yesu Kristu, kamodzi, kwatha. Ndipotu wansembe ali yense amaima tsiku ndi tsiku, natumikira, napereka nsembe zomwezi kawiri kawiri, zimene sizikhoza konse kucotsa macimo; koma Iye, m’mene adapereka nsembe imodzi cifukwa ca macimo, anakhala pa dzanja lamanja la Mulungu cikhalire; kuyambira pomwepo alindirira, kufikira adani ace aikidwa akhale mpando ku mapazi ace. Pakuti ndi cipereko cimodzi anawayesera angwiro cikhalire iwo oyeretsedwa.”
“Ndi cifuniro cimeneco tayeretsedwa mwa copereka ca thupi la Yesu Kristu, kamodzi, kwatha.”
Zindikirani kuti ichi chinalembedwa mu mthawi yatsopano osati mu mthawi yamtsogolo.
Kuti tikhale oyeretsedwa kwanthunthu, ife tonse tiyenera kukhulupilira mu chiombolo cha madzi ndi Mzimu chimene Yesu anapereka kwa ife.
YESU ANAPEREKA CHIOMBOLO CHOSATHA KAMODZI KOKHA
Kodi n’chifukwa chiani munthu ayenera kukondwera nthawi zonse? (1 Atesalonika 5:16)
Chifukwa chakuti Yesu anachotsa machimo ake onse,sangathe koma kuzichepetsa pamaso pa Iye ndi kumthokoza chifukwa cha chisomo Chake.
Ngati takhulupilira mu chiombolo chosatha cha Yesu, takhala olungama tonse kamodzi kokha. Baibulo limanena kuti, “Kondwerani nthawi zonse; Pempherani kosaleka. M’zonse yamikani” (1 Atesalonika 5:16-18).
Kondwerani nthawi zonse. Kodi tingakondwere bwanji nthawi zonse? Iwo amene akulandira chiombolo chosatha kamodzi kokha angasangalale kosatha chifukwa ali omasuka ku uchimo. Iwo ndi otetezedwa mu nzeru zakuti Yesu ananyamula machimo awo onse pa Yordano. Iwo amakhala ozichepetsa pamaso pa Iye ndipo akuyamikira chisomo Chake ndiponso atha kusangala kopanda kulekeza.
“Odala iwo amene okhululukidwa kusayeruzika kwao, nakwiriridwa macimo ao” (Aroma 4:7). Izi sizikutanthauza kuti machimo athu anakwiriridwa ngakhale kuti akupezekabe mu mtima yathu. Mitima yathu inayeretsedwa. Yesu anatsuka kwanthunthu machimo athu onse ndi kutipulumutsa tonse kamodzi kokha.
Chiombolo chosathachi chikusonyezedwa mu Chipangano Chatsopano. Pamene Yesu anabatizidwa, Iye anati, “Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero” (Mateyu 3:15).
Monga mbuzi kapena nkhosa zikunyamula machimo ya anthu kudzera mu kuika manja mu Chipangano Chakale, Yesu ananyamula machimo onse a dziko ndi kuyeretsa mtundu wa anthu mu njira yabwino komanso yoyenera.
“pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero,” Yesu anatero. Yesu anabatizidwa mu njira yoyenera kwambiri ndi kunyamula pa Iyeyekha machimo onse a mtundu wa anthu, motero anapulumutsa ife.
Mu Mateyu 3:15, kunalembedwa kuti Yesu anachotsa machimo onse a dziko. Chilungamo cha Mulungu ndi chanthunthu. Sitiyenera kuyesa kuzindikira chiombolo ichi chosatha. Tiyenera kuwaona ngati mawu Ake a kuombola. “Wodala munthuyo wokhululukidwa chimo lace; wokwiriridwa coipa cace” (Masalimo 32:1).
Machimo onse a mtima ndi thupi, Yesu anawatsuka onse pamene anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi pa Mtsinje wa Yordano. Iye anaweruzidwa chifukwa cha machimo tinachita mu dziko lachinyengo ndi loipali. Pambuyo pakunyamula machimo athu onse, Iye anafa pa Mtanda.
Aliyense amene akhulupilira mu chiombolo cha uchimo chimenechi angakhale olungama ndiponso opanda chilema kamodzi kokha. Chifukwa Yesu akukhala kosatha, aliyense amene akhulupilira mu chiombolo cha Yesu amakhala olungama.
Tsopano tingaime pamaso pa Mulungu ndi chilimbikitso ndi kunena kuti, “Kodi mulibwanji, Ambuye? Ndikhulupilira mwa Mwana Wanu obadwa Yekha, Yesu Kristu ndipo inenso ndine mwana Wanu. Zikomo, Atate. Zikomo chifukwa cha kundivomera kukhala mwana Wanu. Ichi sichifukwa cha ntchito zanga, koma kudzera kokha mu chikhulupiliro changa cha kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu mwa Yesu. Munandipulumutsa ku machimo onse a dzikoli. Ndikukhulupilira zonse zimene munanena, ‘Pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero’ (Mateyu 3:15). Kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi Mtanda Wake, Ndakhala mwana Wanu. Chifukwa cha icho ndili oyamika kwa Inu.”
Kodi munapereka machimo anu onse kwa Yesu? Kodi machimo anu onse anatengedwa ndi Iye? Baibulo limatiuza kuti zikomo ku ubatizo wa Yesu ndi imfa Yake ya pa Mtanda, ochimwa angakhale oyeretsedwa pokhulupilira mwa izo.
UBALE PAKATI PA UBATIZO WA YESU NDI CHIOMBOLO
Kodi pali ubale otani pakati pa ubatizo wa Yesu ndi chiombolo?
Ubatizo wa Yesu ndi chifaniziro cha chiombolo unaneneredwa kudzera mu kuika manja kwa m’Chipangano Chakale.
Taganizani munthu amene akukhala ngati ochimwa ngakhale kuti akukhulupilira mwa Yesu ndi kupemphera mu mpingo, “Okondedwa Mulungu, chonde ndikhululukireni pa machimo amene ndinachita sabata latha. Ndikhululukireni pa machimo a masiku atatu apitawa. O Ambuye, ndikhululukireni chifukwa cha machimo a tsiku lalero. Ndikhulupilira mwa Yesu.”
Tiyeni tiyerekeze kuti munthu ameneyu anakhululukidwa machimo ake a masiku onse ndi pemphero limenelo. Koma kuchoka apo, akupitanso ku moyo wake wamasiku onse ndi kuchimwanso. Ndiyeno, adzakhalanso ochimwa.
Yesu anakhala Mwana wa nkhosa wa Mulungu ndi kuchotsa machimo a ochimwa kudzera mu ubatizo Wake ndi kuwaombola mwa kupachikidwa pa Mtanda. Kuti aomboledwe, ochimwa ayenera kukhulupilira muzotsatirazi kuti aomboledwe.
Uchimo onse unachotsedwa ndi Yesu pamene anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi, motero anakwaniritsa chilungamo cha Mulungu. Machimo onse a dziko anatsukidwa. Aliyense amene wakhulupilira mu choonadi chimenechi ndi oomboledwa. Monga analembera mu Mateyu 3:13-17, “motero” Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi ndi kupanga Mpulumutsi wa okhulupirira onse.
Uthenga wabwino wa choonadi ukutiuza kuti Yesu anachotsa machimo a dziko kamodzi kokha. Koma zaumulungu zabodza zikutiuza kuti timaomboledwa masiku onse. Kodi tikhulupilire ziti? Kodi tinaomboledwa kamodzi kokha, kapena timaomboledwa masiku onse?
Ndi zoonekeratu kuti Yesu anaombola ife kamodzi kokha. Chikhulupiliro choona ndi kukhulupirira mu chiombolo cha madzi ndi Mzimu cha kamodzi kokha. Iwo amene akukhulupilira kuti tiyenera kuomboledwa masiku onse sadzaomboledwa.
Ayenera kudziwa kuti chiombolo choona chikuchokera mu kukhulupilira kuti Yesu anaombola ife kamodzi kokha kudzera mu ubatizo ndi imfa ya pa Mtanda. Chimene tiyenera kuchita ndi kupereka chiyamiko kwa Mulungu ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino oona umenewu.
Koma iwo amene akusocheretsedwa mu chikhulupiliro chawo amanena kuti timaomboledwa ku tchimo loyamba lokha, koma tiyenera kuomboledwa masiku onse ku machimo a tsiku ndi tsiku, ndiponso kuti “pang’ono pang’ono” tingakhale olungama. Izo ndi zolakwika.
Ubatizo wa Yesu ndi imfa Yake ya pa Mtanda zinakwaniritsa chikhululukiro cha uchimo kamodzi kokha. Izi ndi zoonadi. Machimo athu anayenera kupatsidwa kwa Yesu kudzera mwa Yohane Mbatizi ndipo Yesu anayenera kufa pa Mtanda kotero kuti ife tipulumutsidwe.
Kunena kuti “ndikhululukireni” pambuyo pakuti tachimwa sikuyenera Chilungamo cha Mulungu. Lamulo la Mulungu likunena kuti mphotho yauchimo ndi imfa. Tiyenera kudziwa kuti Mulungu ndi chilungamo ndiponso Oyera.
Iwo amene apemphera kwa Mulungu, “Ndine olakwa, chonde ndikhululukireni” akachimwa sadziwa Chilungamo cha Mulungu. Iwo amapempha chikhululukiro, koma mongotsitsimutsa chikumbu mtima chawo. Kodi ndikoyenera kuti munthu achimwa masiku onse ndi kutonthoza chikumbumtima chake mwa kulapa mobwerezabwereza chifukwa cha zolakwa zake? Njira yokhayo yowomboledwera ndi kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda. Tiyenera kukhulupilira mu mitima yathu. Ndi njira yokhayo imene tingapewere chiweruzo cha Mulungu.
Tiyeni tiganize kwambiri pa kuomboledwa ku uchimo. Ahebri 9:22 anena kuti, “Ndipo monga mwa cilamulo zitsala zinthu pang’ono zosayeretsedwa ndi mwazi, ndipo wopanda kukhetsa mwazi kulibe kumasuka.”
Mogwirizana ndi lamulo lachilungamo la Mulungu, machimo ayenera kuchotsedwa ndi mwazi, ndipo popanda kukhetsa mwazi kulibe chikhululukiro. Ili ndi lamulo lachilungamo la Mulungu. Popanda kulipira mphotho ya uchimo, sikukanakhala chikhululukiro.
Lamulo la Mulungu ndi lolungama. Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi ndi kukhetsa mwazi pa Mtanda kuti aombole ife ochimwa. Iye anachotsa zolakwa zathu zonse kudzera mu ubatizo Wake ndi kukhetsa mwazi pa Mtanda kuti alipire machimo athu onse. Iye analipira mphoto ya uchimo m’malo mwathu.
Kodi chiombolo chimaperekedwa kamodzi kokha, kapena masiku onse?
Kamodzi kokha. Yesu anachotsa machimo a ochimwa onse kudzera mu ubatizo Wake.
Mu Mateyu 3:15, Pamene Yesu anali kubatizidwa mu njira yoyenera kwambiri, anatsuka uchimo onse kudzera mu ubatizo Wake ndi kufa pa Mtanda kuti aombole ife ku machimo onse a dziko.
Kuti tipemphe chikhululukiro masiku onse kungakhale chimodzimodzi ndi kupempha Iye kuti achotse machimo athu ndi kufa mobwerezanso. Tiyenera zoonadi kuzindikira lamulo lolungama la Mulungu. Yesu sayenera kufa mobwerezabwereza kuti aombole ife ku machimo athu.
Mulungu amaona ngati ndi mwano kwa iwo amene akhulupilira mwa Yesu kuti azifunsa mobwerezabwereza za chikhululukiro cha machimo atsiku ndi tsiku. “Awa amwano opusa! Akufunsa Mwana Wanga, Yesu, kuti abatizidwe kachiwiri ndi kufa kobwereza pa Mtanda! Akukhulupilira mu chiombolo cha Yesu ndipo akuzitchulabe okha kuti ochimwa! Ndizawaweruza ndi lamulo Langa Lolungama ndi kuwatumiza onse ku dzenje lamoto la gehena. Kodi mukufuna kupha mwana wanu obadwa yekha kachiwiri? Mukuuza Ine kuti ndiphe Mwana Wanga mobwereza chifukwa cha machimo anu atsiku ndi tsiku. Ndinapha kale Mwana Wanga kuti ndipulumutse inu kamodzi ku machimo onse a dziko. Choncho osadzutsa mkwiyo wanga mwa kundifunsa kuti ndikhululukire machimo anu atsiku ndi tsiku, mobwerezabwereza. Ingokhulupilirani mu uthenga wabwino wa chiombolo wa madzi ndi Mzimu.”
Yesu anauza iwo amene akhalabe ochimwa kuti ayenera kupita ku mpingo umene uthenga wabwino oona ukulalikidwa, asiye chikhulupiliro chabodza ndi kulandira chiombolo mwa kugonjetsa chonama ndi chikhulupiliro.
Tsopano ndi nthawi yanu kuti mupulumutsidwe mwa kukhulupilira mu mtimwa mwanu. Kodi mukukhulupilira?
ZOTSATIRA MU CHIKHULUPILIRO OSATI MU CHOONADI, KOMA MU ZINTCHITO
Kodi n’chifukwa chiani Akristu akulephera kupitiliza ndi moyo wachikhulupiliro?
Chifukwa akudalira pa ntchito za iwo okha
Ngakhale ochimwa amene akhulupilira mwa Yesu koma sanaomboledwe angawale mobiliwira kwa zaka zitatu kapena zisanu. Amakhala ofunitsitsa poyamba, koma chikhulupiliro chawo chimachepa popita kwa nthawi. Ngati mukukhulupilira mwa Yesu kudzera mu ntchito zanu, kufunitsitsa kwanu kudzasowanso posachedwa.
Akhungu sangaone, choncho amadalira pa nzeru zawo ndi kupeza nzeru m’njira imeneyi. Pamene amvera misozi ikuchoka, amalakwitsa poganiza kuti ndi chizindikiro cha chikhululukiro. Chikhululukiro choona si chomvera.
Akhungu auzimu amafuna kupeza chikondi chawo choyamba mwa kupezeka pa msonkhano obwereza mwachabe, koma sangapeze kumvera kwawo. Chikhululukiro cha uchimo ndi chovutanso kuchipeza. Ngati anakhulupilira moyenera poyamba, chikhululukiro ndi chisomo Chake chingawale mobwiliwira kwambiri pamene masiku akupita.
Koma chikhululukiro chonama chimawala poyamba pokha ndipo chimataya kuwala kwake kuchokera pamenepo mkuka mtsogolo. Kuwala kwachangu kumasowa posachedwa chifukwa akhungu auzimu amalephera kumvera uthenga wabwino oona kuyambira pachiyambi.
Alembi ndi Afalisi onyenga amanyamula Mabaibulo mkhwapa mwawo, kuika pa mtima pemphero la Ambuye ndi chikhulupiliro cha Atumwi, ndi kupemphera nthawi zonse. Amapatsidwa maudindo mu mpingo ndipo amakhala udzikudza. Koma machimo awo amakula ndipo pomaliza amachotsedwa ndi Mulungu. Kunja ali ophimbidwa ndi pulasitala loyera la chifuno cha chipembedzo, koma mkati mwa maganizo awo ndi movunda ndi uchimo. Ichi ndi chifukwa cha chikhulupiliro osati mu choonadi koma mu chipembedzo chochokera mu ntchito zawo.
TIMAKHALA OLUNGAMA MWA CHIKHULUPILIRO
Kodi chiombolo cha uchimo m’dzikoli chinakwaniritsidwa kale?
Inde. Chinakwaniritsidwa kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi imfa Yake pa Mtanda.
Tiyeni tsopano tiwerenge Ahebri 10:16-18. “Ici ndi cipangano ndidzapangana nao, atapita masiku ajawo, ananena Ambuye: Ndidzapereka malamulo anga akhale pamtima pao; ndipo pa nzeru zao ndidzawalemba; ndipo macimo ao ndi masayeruziko ao sindidzawakumbukilanso. Koma pomwe pali cikhululukiro ca macimo palibenso copereka ca kwa ucimo.”
Tsopano popeza tinaomboledwa kudzera mu madzi a ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda, sitiyeneranso kudzitetezera ku machimo. Chingamveke chodabwitsa pamene mwamva poyamba, koma ndi mogwirizana ndi mawu a Baibulo. Kodi awo ndi mawu a mtundu wa anthu? Baibulo ndiye likulu ndiponso chingwe champhamvu choyezera chili chonse.
“Ndidzapereka malamulo anga akhale pamtima pao; ndipo pa nzeru zao ndidzawalemba” (Ahebri 10:16). Kodi munamva bwanji pambuyo pakuti mwaomboledwa? Tsopano popeza mtima wanu ndi omasuka ku uchimo, mukumva kukoma. Mwakhala munthu olungama ndipo mungakhale mu kuunika.
Ndipo Ambuye anati mu Ahebri 10:17 “Ndipo macimo ao ndi masayeruziko ao sindidzawakumbukilanso.” Iye akutiuza kuti sadzakumbukilanso machimo ndi zolakwa za woomboledwa. Chifukwa chiani? Chifukwa chakuti Yesu anabatizidwa mu njira yoyenera kwambiri, “motero.” Pambuyo pa kuchotsa uchimo onse, Yesu anaweruzidwa m’malo mwa iwo amene akhulupilira mwa Iye.
Tsopano popeza analipira machimo athu onse, tingawakumbukile koma sitifunika kumamva kuti ndife amilandu chifukwa cha iwo. Sitizafanso chifukwa cha machimo athu chifukwa Yesu anatsuka uchimo onse ndi kukhetsa mwazi wake pa Mtanda m’malo mwathu.
Ahebri 10:18 anena kuti “Koma pomwe pali cikhululukiro ca macimo palibenso copereka ca kwa ucimo.” Ichi chikutanthauza kuti Iye anachotsa machimo onse a dziko. Chikutanthauzanso kuti iwo amene anabadwanso mwa Yesu sayeneranso kupanga chopereka cha uchimo.
“O Mulungu wanga, chonde ndikhululukireni ine. Chifukwa chimene ndimakhulupilira mwa Yesu ndipo ndikukhala m’masautso ndi chakuti ndikalibe kuomboledwa. Ndine Mkristu, koma maganizo anga anavunda kotheratu ndi uchimo.” Sitiyenera kupemphera motero.
Ochimwa amachita uchimo popanda kuzindikira motero. Iwo sadziwa kuti uchimo ndi chiani chifukwa sadziwa Lamulo la Mulungu la Choonadi. Iwo amangodziwa kuti sayenera kuchimwa mu chikumbumtima chawo koma sadziwa kuti kuchimwa ndi chiani pamaso pa Mulungu. Mulungu analozera kwa ife kuti ndi kuchimwa kusakhulupilira mwa Yesu.
Mu Yohane 16:9 ananena kuti kuchimwa ndi chiani pamaso pa Mulungu. “Za macimo, cifukwa sakhulupirira ine.” Ndi kuchimwa pamaso pa Mulungu kusakhulupilira mwa Iye. Yohane 16:10 akunena kuti chilungamo ndi chiani. “Za cilungamo, cifukwa ndinka kwa Atate, ndipo simundionanso” M’mawu ena, Yesu anaombola kale dzikoli ku uchimo onse, ndipo motero sayeneranso kutiombola mobwereza ndi ubatizo wachiwiri ndiponso imfa yake pa Mtanda.
Iye anaitana iwo amene akhulupilira mu chiombolo kuti awayeretse ndi kuwapanga iwo olungama. Chiombolo m’dzikoli chinatsirizika kudzera mu ubatizo Wake ndi imfa ya pa Mtanda. Palibenso chiombolo china chimene chikufunikira kuti chiombole ochimwa.
“Pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.” (Machitidwe a Atumwi 4:12). Yesu anabwera ku dzikoli, anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi, ndi kukhetsa mwazi wake pa Mtanda kuti aombole ochimwa onse. Khulupilirani zimenechi mu mtima mwanu ndi kupulumutsidwa. Yesu anayeretsa inu ndi madzi komanso Mzimu.
Yesu anasesa machimo onse akuthupi lathu kudzera mwa madzi ndi Mzimu. Tinapulumutsidwa ndi chikhulupiliro. Ngati tikhulupilira mu choonadi, ngati tikhulupilira mu uthenga wabwino kudzera mwa Yesu Kristu, timakhala olungama kamodzi kokha. Ubatizo wa Yesu ndi imfa Yake pa Mtanda; zinthu ziwiri zimenezi zikusonyeza choonadi chenicheni.
NDIME ZIMENE OCHIMWA AKUGWIRITSA NCHITO NGATI POBISALIRA PAWO
Kodi tingaomboledwedi mwa kuvomereza machimo athu, kapena tinaomboledwa kale?
Mulungu anapereka chiombolo cha uchimo kamodzi kokha
1 Yohane 1:9 anena kuti, “ngati tibvomereza macimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire macimo athu, ndi kutisambikatsa kuticotsera cosalungama ciri conse.”
Kukanakhala bwino ngati kunali koyenera kungobvomereza machimo athu kuti tikhululukidwe. Ndi chimenechi m’maganizo athu, ophunzitsa zaumulungu ena anadza ndi ganizo labwino la chiphunzitso chatsopano. Iwo akukakamira kuti nthawi zonse pamene munthu wavomereza machimo ake angakhululukidwe. Kodi icho sichoyenerera? Koma Yesu sananene kuti tingakhululukidwe nthawi zonse pamene taulula tokha kwa Mulungu.
Kodi tingakhululukidwedi zoona mwa kungovomereza machimo athu, kapena tinaomboledwa kale? Kodi ndi chiani chimene mumakhulupilira? Anthu amene akunenera chiphunzitso chabodza chimenechi akukhulupilira kuti amakhululukidwa nthawi zonse pamene aulula machimo awo, koma zoona zake, uchimo umakhalabe mu mitima yawo chifukwa sadziwa mawu oona a chiombolo. Si za nzeru kuti ochimwa amene akhulupilira mwa Yesu amakhululukidwa nthawi zonse pamene apempha chikhululukiro cha machimo atsiku ndi tsiku.
Pachifukwa ichi, tiyenera kumvetsera mawu Ake a chiombolo ndi kusiyanitsa pakati pa choonadi ndi chonama, kupatula zimene tinauzidwa.
Ochimwa samvetsetsa 1 Yohane 1:9. Iwo molakwa amaganiza kuti zikukhudza chikhululukiro cha machimo a masiku onse. Tiyeni tiwerenge ziphunzitso mwatcheru. “Ngati tibvomereza macimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire macimo athu, ndi kutisambitsa kuticotsera cosalungama ciri conse.” Kodi muganiza kuti tingapulumutsidwe ku tchimo loyamba lokha ndipo kuti tiyenera kuulula machimo athu atsiku ndi tsiku kuti Iye akhale okhulupirika ndi olungama kuti akhululukire machimowo? Awa ndi maganizo osalondola bwino amene amachokera ku zofoka za thupi lathu.
Tikuzindikira kuti izi sizoona pamene takhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Uchimo onse unatsukidwa kale ndi ubatizo Wake komanso mwazi wa pa Mtanda kale, kalekale kwambiri.
Kukhulupilira mogwirizana ndi Mzimu ndi kukhulupilira mogwirizana ndi maganizo osalondolo ndi zinthu ziwiri zosiyana. Iwo amene amakhulupilira mogwirizana ndi maganizo zwo amamva kufunika kwa kutsuka machimo awo masiku onse, koma iwo amene akhulupilira mu chiombolo cha madzi ndi mwazi akudziwa kuti anaomboledwa kale kamodzi kokha kudzera mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu Kristu.
Iwo amene akhulupilira kuti ayenera kuvomereza masiku onse kuti aomboledwe mwatsopano ndi amene akuchita uchimo wa kusakhulupilira mu chiombolo kudzera mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu.
Kodi munaomboledwa kamodzi kokha kudzera mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu? Iwo amene sanaomboledwe amayesa kupindula chipulumutso mwa kuvomereza machimo awo masiku onse. Izi zikusiyabe vuto la zimene angachite ndi machimo atsiku ndi tsiku amene adzachite mtsogolo.
Angayese kuululilatu machimo awo amtsogolo. Koma kuchita choncho akuonetsa kuchepekera kwa chikhulupiliro chawo mwa Yesu. Anthu amenewa ndi akhungu ku uthenga wabwino wa chiombolo. Yesu anaombola ife ku uchimo kamodzi kokha ndi ubatizo Wake ndiponso mwazi, kunyamula chiweruzo pa Iyeyekha. Ndife owomboledwa kokha chifukwa cha kukhulupilira mwa Iye.
Ngati muganiza kuti muyenera kuulula ngakhale machimo anu a mtsogolo kuti mupulumutsidwe, ndinu ofanana ndi osakhululupirira amene sadziwa kanthu pa kubadwanso mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Ochimwa sangaomboledwe kudzera mu kuvomereza.
Motero ngati mungaulule mokhulupirika, “Ndine ochimwa amene sindinaomboledwe,” ndipo ndiyeno ngati mungamvetsere ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino wa ubatizo Wake ndi imfa ya pa Mtanda, Mulungu adzakuombolani inu ku machimo anu onse.
Koma ngati simukhulupilira mu uthenga wabwino wachiombolo ndi kubisala kunsi kwa mapemphero a kulapa, mudzaona chiweruzo chowawa pamene Yesu adzabwerenso ku dzikoli ngati Oweruza Olungama.
Iwo amene sakhulupilira mu chiombolo cha uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu adzaweruzidwa. Ngati akubisala kuseri kwa kulapa, adzaona chiweruzo . Choncho, musayembekezere tsiku la chiweruzo. Khulupilirani tsopano mu uthenga wabwino odalitsika wa madzi ndi Mzimu.
KUVOMEREZA KOYENERA NDI CHIKHULUPILIRO CHOONA
Kodi kuvomereza kwabwino kwa ochimwa ndi kotani?
Kuvomereza kuti adakali ndi uchimo ndipo adzapita ku gehena pokhapokha ngati wakhulupilira mu uthenga wabwino oona
Mulungu anatiombola kamodzi kokha. Ichi ndi chitsanzo cha chochitika-choona chofotokoza zimene ndikuyesa kunena. Tiyeni tiyerekezere kuti m’zondi wa ku Mpoto kwa Korea akutsikira ku Mwera kwa Korea. Akuona m’mene tili ochitira bwino, wazindikira kuti ananyengedwa, ndi kuganiza kuti adzipereke yekha.
Atapita pa malo a apolisi apafupi, atha kuvomereza motere, kunena kuti, “Ndine m’zondi wa ku mpoto,” kapena “ndinachokera kumwera kuzapha akuti ndi akuti, ndi kuphulitsa ichi ndi icho, ndipo ndinaphulitsa kale ichi, koma tsopano ndikudzipereka ndekha. Motero sindilinso m’zondi.”
Kodi uku ndi kuvomereza koyenera? Ngati anali kufuna kuti aulule zoona, zimene anayenera kunena ndi zakuti “ Ndine m’zondi.” Ndemanga imeneyi ikusonyeza zonse: kuti ndi munthu oipa ndipo ndioyenera kuweruzidwa. Ndi ndemanga yosavuta imeneyo, zilibe kanthu kuti anadzera ntchito yotani, angamasulidwe.
Chimodzimodzinso , ngati ochimwa wavomereza pamaso pa Mulungu, “ndine ochimwa amene sindinaomboledwe. Ndine oyenera kuponyedwa ku gehena ndi kuweruzidwa. Chonde ndipulumutseni” ndi kukhulupilira mwa Yesu, adzaomboledwa. Yesu anabatizidwa ndi kukhetsa mwazi m’malo mwathu, ndipo chimene tiyenera kuchita ndi kukhulupilira mu chipulumutso kudzera mwa Iye kuti tipulumutsidwe.
Chibvumbulutso 2:17 anena kuti, “Ndipo ndidzampatsa mwala woyera, ndip mwalawo ndzina latsopano lolembedwapo, wosalidziwa munthu ali yense koma iye wakuulandira.” Baibulo linena kuti yekhayo amene akulandira uthenga wabwino oona ndi amene adzadziwa dzina la Yesu. Yekhayo amene anaomboledwa kamodzi kokha akudziwa chinsinsi cha kukhala olungama.
Iwo amene sadziwa zimenezi adzakhalabe ochimwa ngakhale amapemphera mapemphero akulapa masiku onse. Kuvomereza sikutanthauza kupempha chikhululukiro masiku onse. Ngakhale kuti munthu wakhala Mkristu kwa zaka khumi, adzakhalabe ochimwa ngati akupempha chikhululukiro kwa Mulungu masiku onse. Iye sadzakhala mwana wa Mulungu.
Kuti apulumutsidwe anayenera kuvomereza kuti ndi ochimwa ndi kukhulupilira mu chiombolo cha mwa Yesu. Ichi ndi chikhulupiliro choona.
KUNDANDAMIKA MACHIMO A MUNTHU SICHIMENE 1 YOHANE 1:9 IKUTIUZA ZA KUVOMEREZA
Kodi tiyenera kuvomereza machimo athu masiku onse, kapena kamodzi kokha kuti tipulumutsidwe?
Nthawi imodzi yokha
Kodi mbala ndi wakupha angavomereze zochita zawo ndi kuomboledwa? Ochimwa saomboledwa mongovomereza machimo awo. Angaomboledwe kokha kudzera mu dalitso la uthenga wabwino wa kubadwanso mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu mwa Yesu.
Akristu ena osochera amaulula motere. “Mulungu okondedwa, ndakangana ndi winanso lero. Ndachimwa. Ndachita chinyengo. Ndinaba chinthu china.”
Ngati angapitilize motero Mulungu anganene kuti, “khala chete, iwe ochimwa! Nde chiani?”
“Chonde pitilizani kumvera kwa ine. Mulungu, munatiuza kuti tiulule machimo athu. Ndikupempha chifundo Chanu.”
Pemphero lotere ndi limene Mulungu safuna kulimva. Iye akufuna kumvera mapemphero a iwo amene akhulupilira mu chiombolo cha madzi ndi Mzimu: Iwo amene avomereza machimo awo ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino woona wa kubadwanso mwatsopano.
Augustini ananena kuti analapa pamene ankayamwa mawere a amai ake. Anaganiza kuti kuvomereza kotereko kudzamupereka ku Ufumu wa Kumwamba. Tingaseke chabe pa zimenezi. Kuvomereza kokha machimo a munthu sikungathandize.
Mulungu akuti, “Khala chete ndipo ndiuze chabe ngati unachimwapo. Ngati unatero, ndiyeno siya kuyankhula za zimenezo. Wakhala ukukhulupilira molakwika mpaka tsopano, tsono yenda ku mpingo umene amaphunzitsa choonadi Khulupilira mu uthenga wa chiombolo m’njira yoyenera ndipo khala woomboledwa. Ngati sunatero, ndizabwera kudzaweruza iwe.”
Mapemphero a kulapa a chikhululukiro ndi zina zoyesa kuti mupulumutsidwe kudzera mu kuvomereza zikusonyeza chikhulupiliro chosalondola ndiponso chabodza.
Kunalembedwa mu 1 Yohane 1:9 kuti ngati tivomereza machimo athu onse, uthenga wabwino wa madzi ndi mwazi udzatiombola ku uchimo wathu onse.
“CHOKA KWA INE”
Kodi kuchita kusayeruzika Kukutanthauza chiyani?
Kukutanthauza kukhulupirira mwa Yesu ndi uchimo mu mtima mwamunthu.
Akristu ochimwa ali ndi chikhulupiliro chosochera, akuchita zolakwika pamaso pa Yesu. “Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mau m’dzina lanu, ndi m’dzina lanunso kuturutsa mizimu yoipa, ndi kucita m’dzina lanunso zamphambvu zambiri? Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo sindinakudziwani inu nthawi zonse; chokani kwa Ine inu akuchita kusayeruzika.’” (Mateyu 7:22-23)
Ganizirani kuti munthu amene akhulupilira mu zabodza wafa, wabwera ndi kuima pamaso pa Mulungu, ndi kunena kuti, “Kodi munali kuti, Ambuye? Munali kuoneka okongola pamene ndinali kukuganizirani pansi paja. Koma mukuoneka okongola koposa ngakha kuno. Zikomo, Ambuye. Munandipulumutsa ine. Ndikukhulupilira kuti mukuona ine ngati opanda tchimo ngakhale kuti ndilibe ndi tchimo mu mtima mwanga. Ndabwera kuno chifukwa Inu munandilonjeza kuti muzanditenga kupita Kumwamba. Tsopano ndidzapita kumeneko kumene maluwa akunyezimira kosaneneka. Nda-pita ndipo ndili ndi chiyembekezo kuti ndizakuonani pompano.”
Wayamba kupita chakumunda, koma Yesu wamuimitsa iye. “Tayembekeza! Tiyeni tione ngati munthu uyu ali ndi uchimo mu mtima mwake. Kodi ndiwe ochimwa?”
“Indedi ndili ndi uchimo. Koma kodi sindinakhulupire mwa Inu?”
“Kodi uli ndi uchimo ngakhale kuti ukhulupilira mwa Ine?”
“Inde, ndili ndi uchimo.”
“Chiani? Uli ndi uchimo? Tandipatsani Buku la Moyo. Ndiponso tandipatsaninso Buku la Ntchito. Taonani dzina lake. Onani ndi Buku liti limene muli dzina lake.”
Kunena zoona, dzina lake lili mu Buku la Ntchito.
“Tsopano, ulula machimo amene unachita padziko lapansi.”
Munthuyo anayesa kuti asatero, koma Mulungu anamukakamiza kuti atsekule kamwa lake ndi kuvomereza machimo ake.
“Inde, ndinachita machimo otere ndi otere…”
Iye anasokonezeka ndipo sanathe kutseka kamwa lake.
“Chabwino, zimenezo zakwana! Wachita zambiri zoyenera ku gehena. Iye ndi oyenera kopambana kuchita bwino. Muperekeni ku malo otentha.”
Iye sanaperekedwe kumalo komwe kuli maluwa odzala ndi kunyezimira, koma kumalo kumene ndi kodzala ndi moto wasulfule. Iye akukukuta mano ake pamene akuperekedwa ku gehena.
“Ndinakhulupilira mwa Inu, ndinanenera m’dzina Lanu, ndinalalikira m’dzina Lanu, ndinagulitsa nyumba yanga kuti nditumikire inu, ndinathandiza amasiye, ndinapilira kwambiri m’dzina Lanu, ndinali kupemphera madzulo, kuchiritsa odwala… ndikuyenera kupita Kumwamba.”
Akukukuta mano ake kwambiri kotero kuti akuwagwetsera pachabe. Pamene wafika ku gehena, anaona Akristu onse amene sanadziwe tanthauzo loona la chiombolo cha Yesu. Iwo amene sanazindikire bwino uthenga wabwino wa chiombolo anasiyidwa ndi Iye.
MACHIMO A OKHULUPILIRA ONAMA ANALEMBEDWA MU BUKU LA NTCHITO
Kodi machimo a ochimwa onse alembedwa kuti?
Alembedwa m’mitima yawo ndi mu Buku la Ntchito
Kapena tikukhulupilira mwa Yesu kapena ai, Mulungu amaononga iwo amene ali ndi uchimo mu mitima yawo. Ngati wapeza ngakhale ka tchimo kang’onong’ono mu mtima mwa wina, munthu ameneyo aweruzidwira ku gehena pa Tsiku la Chiweruzo. Mulungu akuchenjeza ochimwa amene sanaomboledwe kuti aulule kuti sanaomboledwe ngati akufuna kuti apeze chiombolo.
Machimo a ochimwa analembedwa mu mtima mwake. Iwo amene ndi obadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu angakumbukire machimo awo, koma amachotsedwa mu mitima yawo. Iwo ndi olungama.
Koma iwo amene sanabadwenso ali ndi uchimo mu mitima yawo. Motero iwo ndi ochimwa pamaso pa Mulungu. Nthawi zonse pamene akugwada kuti apemphere, machimo awo amawapatula kwa Mulungu ndi kuletsa Iye kuti asamve mapemphero awo. Amapemphera pa ichi ndi icho, koma machimo awo amakhalilirabe. Pamapeto pake amaulula machimo awo, kulapa zolakwa zawo zimene anachita zaka khumi zapitazo, zaka khumi n’chimodzi zapitazo, ngakhalenso zaka makumi awiri zapitawo.
Kodi ayenera kulapa mobwerezabwereza m’mapemphero awo? Kodi n’chifukwa chiani amachita zimenezo? Sakufunika kuchita zimenezo, koma pamene ayamba kupemphera, amakumbukira kuti ali ndi mlandu pamaso pa Mulungu. Choncho amamva kuti ayenera kudzitetezera machimo awo asanayambe kupemphera mwakuya kwambiri.
Mulungu analemba machimo awo ndi bopeni yachitsulo pansi pa mitima yawo kotero kuti machimo awo asafufutidwe. Mwa ichi, amamva kuti ayenera kuvomereza machimo awo nthawi zonse pamene abwera pamaso pa Mulungu. Choncho iwo amene akhulupilira mu theka lokha la uthenga wabwino wa Yesu ayenera kukhala m’mavuto ngati ochimwa ndi kuthera mu gehena.
Mu Yeremiya 17:1, kunalembedwa kuti, “Cimo la Yuda lalembedwa ndi peni lacitsulo, ndi nsonga ya diamond; lalembedwa pa colembapo ca m’mtima mwao, ndi pa nyanga za maguwa a nsembe anu.”
Yuda ndi dzina la mtundu wachifumu wa anthu a Israyeli. Baibulo linaika Yuda kuimira mtundu onse wa anthu, choncho Yuda akutanthauza anthu onse.
Uchimo wa Yuda unalembedwa ndi peni ya chitsulo ndi kulembedwa ndi nsonga ya diamondi chimene chingadule kupyolera mu chitsulo. Diamondi ndi chiwiya cholimba koposa m’dziko lonse. Ndi peni ya chitsulo ndi nsonga ya diamondi machimo athu analembedwa.
Pamene alembedwa, sangachotsedwe. Sazachotsedwa pokhapokha ngati takhulupilira mu choonadi cha madzi ndi Mzimu.
Ndi kupanda ntchito kuomboledwa m’maganizo mwawo, kukhulupilira mu ziphunzitso za Chikristu, kuika pamtima zaumulungu, ndi kuziika okha ku mpingo ngati uchimo udakali mu mitima yawo.
Popeza machimo awo sangachotsedwa popanda ubatizo wa Yesu, ochimwa amapitiliza kukumbukira iwo, akunena kuti, “Ambuye, ndine ochimwa,” nthawi zonse pamene akupemphera. Adakali ndi uchimo m’mitima yawo komabe amayesera kukhala ndi chiyanjano ndi Mulungu, kukhala ndi maudindo ochuluka mu mpingo, ndi kuphunzira zaumulungu ndiponso chiphunzitso kwambiri.
Choncho amapita ku mapiri, kuyesa kumanenera m’malilime pachabe ndi kusaka masomphenya a Malawi a moto, koma zonse ndi zopanda ntchito. Ngati uchimo ukadali mu mtima wanu, simudzakhala pa mtendere.
Uchimo wathu, monga analembera mu Yeremiya 17:1, unaikidwa pa nyanga za pa maguwa athu. Kumwamba, kuli Buku la Moyo ndi Buku la Ntchito. Machimo a ochimwa amalembedwa mu Buku la Ntchito ndipo motero anthu sangathawe zolakwa zawo. Mulungu amazilemba mu Buku la Ntchito ndiponso mkati mwa chikumbumtima chathu ndi kuzionetsa kwa ife kudzera mu lamulo Lake.
Tiyenera kuchotsa zolembedwa zimenezi kukhala zoyera mwa kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi umene anakhetsa m’malo mwathu ndi kutipulumutsa. Ndiyeno tizakhala okonzekera pa moyo osatha, ndipo maina athu adzalembedwa mu Buku la Moyo.
KODI DZINA LANU LILIMO M’BUKU LA MOYO?
Kodi ndi dzina la ndani linalembedwa mu Buku la Moyo?
Maina a iwo amene alibe uchimo mu mitima yawo ndi amene analembedwa m’menemo.
Ndi kofunikira kuti dzina lanu lilembedwe mu Buku la Moyo. Ngati kuti dzina lanu silinalembedwe m’menemo, kodi pali phindu lanji lakukhulupilira mwa Yesu? Kuti muomboledwe moona, muyenera kukhulupilira mu kukhala obadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.
Yesu anabwera ku dzikoli, anabatizidwa pamene anali ndi zaka makumi atatu kuti atsuke machimo onse a dziko, ndi kufa pa Mtanda kuti aombole ife. Monga analembera mu Mateyu 3:15, Yesu “motero” anabatizidwa ndi kupachikidwa pa Mtanda. Tiyenera kukhulupilira chimenechi kuti maina athu alembedwe mu Buku la Moyo.
Pamene anthu akufa ndi kuima pamaso pa Mulungu, Mulungu amati, “Taonani ngati dzina la munthu uyu lili mu Buku la Moyo.”
“Lilimo, Ambuye.”
“Inde, unanzunzika ndi kukhetsa misozi padziko lapansi chifukwa cha Ine, tsopano ndizapanga chonchi kuti usadzachitenso chimenechi mobwereza.”
Mulungu amakhuthulira pa munthu wotere nduwira ya chilungamo ngati mphatso.
“Zikomo, Ambuye. Ndine oyamikira kwamuyaya.”
“Angelo, ikani ndiwira pa munthuyu.”
“Ambuye, kuli kokwanira kuti munandipulumutsa ine. Nduwira ingakhale yaikulu kwambiri kwa ine. Zikomo. Ndine oyamikira kwambiri kuti munandipulumutsa ine. Ndine okhitira kwambiri kukhala kokha pamalo pomwe mupezeka inu.”
“Angelo, gwadani pansi ndipo tengani uyu mwana wanga wa chi 10,000 kumbuyo kwanu.”
Angelo akuyankha, “Inde, Atate.”
“Chonde bwerani kumbuyo kwanga.”
“Ndikumva bwino kwambiri. Kodi ndikuchita molondola sichoncho? Tiye tizipita.”
Angelo amayenda mosamala. Kodi ungakonde kuti uyende?”
“Aha, kuno ndi kokongola kwambiri. Kodi malo anu ndi akulu kotani?”
“Ndakhala ndili kuyenda kuzungulira malo onse kwa zaka mabiliyoni, koma sindinapeze malekezelo ake.”
“Kodi ndi zoona? Muyenera kukhala olema chifukwa cha ine. Muyenera kundiika pansi tsopano.”
“Sititha mphamvu kumwamba kuno.”
“Zikomo, koma ndikufuna kuima pansi pa Ufumu wa Kumwamba. Tsopano kodi olungama onse ali kuti amene anafika pambuyo panga?”
“Iwo ali apo.”
“Tiyeno tifikepo.”
Aleluya! Anakumbatirana ndi kumwetulirana ndi kukhala mokondwa kuchokera pamenepo.
Tsopano taganizirani kuti munthu amene akhulupilira mwa Yesu koma akali ochimwa wafa ndi kuima pamaso pa Mulungu. Iyenso anena kuti anakhulupilira mwa Yesu ndi kuvomereza kuti ndi ochimwa.
Mulungu amati, “Onani ngati dzina la munthuyu linalembedwa mu Buku la Moyo.”
“Silikupezeka mu Buku, Ambuye.”
“Ndiyeno taonani mu Buku la Ntchito.”
“Dzina lake ndi machimo ake zili muno.”
“Ndiyeno perekani munthu ameneyu ku malo kumene sazayenera kuda nkhawa za mtengo wamafuta, ndipo musiyeno akhale kumeneko kwamuyaya.”
“Oho, Ambuye, sikuchita bwino kumeneko…”
Iye akunena kuti sikuchita bwino. Kodi n’chifukwa chiani ayenera kuperekedwa ku gehena ngakhale kuti anakhulupilira mwa Yesu mwaluntha kwambiri?
Chifukwa ndi chakuti ananyengedwa ndi Satana ndipo iye anamvera ku theka lokha lachoonadi cha uthenga wabwino. Ngati sitikumvetsetsa tanthauzo loona la chiombolo cha Yesu, tidzazipeza ku gehena, nafenso.
Munthu uyu anakhulupilira mwa Yesu, koma ananyengedwa ndi Satana ndi kuganiza kuti anali ochimwa. Akanakhala kuti anamva za uthenga wabwino oona, akanazindikira kuti chikhulupiliro chake chinali cholakwika. Koma analephera kukhulupilira chifukwa cha kugwirizana kwake ndi zikhulupiliro zake zolakwika.
Ngati mukufuna kupita ku Ufumu wa Kumwamba, muyenera kukhulupilira mu kubadwanso kwatsopano kwa madzi ndi Mzimu. Monga kunalembedwa mu Mateyu 3:15, “motero” Yesu anachotsa machimo onse a dziko lapansi. Muyenera kukhulupilira mu chipulumutso cha madzi ndi mwazi.
Kodi ndi maina otani amene amalembedwa mu Buku la Ntchito?
Maina a iwo amene li ndi uchimo m’mitima yawo ndi amene amalembedwa m’menemo.
Ngati mwasankha kukhulupilira zilizonse, ngati munthu okula-bwino amene sakana chiitano cha mai ake, mungapite ku gehena. Kuli anthu ambiri okula-bwino ku gehena, koma Kumwamba, kuli omenya oona amene anamenyera zimene akukhulupilira.
Iwo amene ali Kumwamba anadziwa kuti anali ochimwa amene anayenera kupita kugehena ndipo moyamikira anakhulupilira kuti machimo awo anatsukidwa kudzera mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu.
Kunanenedwa kuti kuli milu ya makutu ndi kamwa Kumwamba. Chifukwa anthu ambiri anakhulupilira mu chiombolo cha Yesu ndi kamwa kapena makutu okha, Mulungu amataya thupi lawo lotsala lonse mu moto oyaka wa sulfule.
Taganizani kuti iye amene akhulupilira mwa Yesu koma adakali ndi uchimo mu mtima mwake waima pamaso pa Mulungu ndi kunena kuti, “Ambuye, anthu ananditchula olungama chifukwa ndinakhulupilira mwa Yesu, ngakhale kuti ndinali ndi uchimo mu mtima mwanga. Ndinakhulupilira kuti inunso muzayang’ana kwa ine ndi kundiona ngati opanda tchimo. Icho ndi chimene ndinaphunzira ndiponso chimene ndinakhulupilira. Ndinali kukhulupilira chifukwa anthu ambiri amatero. Chinali chikhulupiliro chodziwika chololedwa dziko lonse kumene ndikuchokera.”
Ambuye amayankha kuti. “Sindingakhululukire iwo amene ali ndi uchimo mu mitima yawo. Ndinatsuka machimo anu onse ndi dalitso la kubadwanso mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Koma munakana kukhulupilira m’menemo. Angelo! Ponyani munthu wamwanoyu mu moto wa gehena.”
Aliyense amene akhulupilira mwa Yesu koma akuganizirabe kuti ali ndi uchimo mu mtima mwake adzapita ku gehena. Mverani ku uthenga wabwino woona wa chiombolo ndipo omboledwani ku uchimo onse. Ngati sichoncho, mungapite kukatenthedwa ku gehena.
Kunena kuti mulibe uchimo pamene muli ndi uchimo mu mtima mwanu ndi kunyenga Mulungu. Tingaone kuti pali kusiyana kwakukulu pakati pa ochimwa ndi olungama pothera pake. Muzazindikira chifukwa chake ndinakupemphani kuti muomboledwe.
Muzaona kusiyana pakati pa iwo amene akukhulupilira mu chiombolo chathunthu (ubatizo wa Yesu ndi imfa Yake ya pa Mtanda) ndi iwo amene sanatero pamene mwaima pa mphambano ya njira ya Kumwamba ndi ku gehena. Chidzapanga kusiyana kwakukulu. Ena adzalowa ku Ufumu wa Kumwamba koma ena adzapita ku gehena.
Kodi mukhulupilira mwa Yesu koma mudakali ochimwa? Ndiyeno muyenera kuzindikira kuti muyenera kubadwanso mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Mulungu akutuma iwo amene ali ndi uchimo mu mitima yawo ku gehena. Okhawo amene akhulupilira mu chikhululukiro chonse cha uchimo ndi amene angalowe mu Ufumu wa Kumwamba.
Chitani tsopano lino. Ngati mungachotse, kungakhale kuchedwa. Khalani okonzekeratu. Musanapite ku gehena, khulupilirani mu chiombolo cha madzi ndi Mzimu ndipo khalani oyeretsedwa.
Ulemero kwa Ambuye wathu Yesu! Tikuyamika Iye chifukwa cha chisomo Chake pakupanga ife ochimwa kukhala oyera. Aleluya!
YESU: NKHOSWE YA WOLUNGAMA
Kodi machimo athu angachotsedwe mwa mapemphero a kulapa?
Ai, ndi kosatheka konse. Uku ndi njira imodzi imene Satana amatinyengera nayo.
Tiyeni tiwerenge 1 Yohane 2:1-2. “Tiana tanga, izi ndikulemberani, kuti musa cimwe. Ndipo akacimwa wina, nkhoswe tiri naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu wolungama; ndipo Iye ndiye ciombolo ca macimo athu; koma osati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.”
Kodi mukuona zimene zalembedwa? Kodi pali wina amene akhulupilira koma adakali ndi uchimo mu mtima mwake? Ngati muli ndi uchimo mu mtima mwanu koma mukuuza Mulungu kuti mulibe, mukumunamizira Iye. Ndipo mukudzinyenganso nokha, inunso.
Koma ngati zoona mukumvetsetsa Yesu ndi kukhulupilira zimene anachita kuti atsuke machimo onse pa Yordano, muzakhala omasuka kwathunthu ku uchimo. Ndiyeno munganene kuti, “Ambuye, Ndinabadwanso mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu mwa Inu. Ndilibe uchimo. Ndingaime pamaso panu popanda manyazi.”
Ndiyeno Ambuye adzayankha. “Inde, ukunena zoona. Monga Abrahamu anakhulupilira mwa Ine ndi kuzikhulupilira yekha kukhala olungama, ndinunso olungama chifukwa ndinatsuka machimo anu onse.”
Koma ganizirani munthu amene adakali ndi uchimo mu mtima wake ngakhale kuti akukhulupilira mwa Yesu. Iye akuti, “Chifukwa ndinakhulupilira mwa Yesu, Ndizapita Kumwamba ngakhale kuti ndili ndi kauchimo kochepa mu mtima mwanga.”
Akufuna kwambiri kuvomerezeka Kumwamba moti akuyesa kukakamira pamene akuima pamaso pa mpando wachiweruzo, koma adzatherabe ku gehena. Chifukwa chiani? Sakudziwa uthenga wabwino wodalitsika wa kukhala obadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.
Aliyense ayenera kuvomereza kuti ndi ochimwa m’masiku ake a padziko lapansi. “Ndine ochimwa. Ndidzapita ku gehena. Chonde ndipulumutseni.” Ochimwa samaomboledwa ndi mapemphero a kulapa. Koma, ayenera kuvomereza kuti ndi ochimwa ndi kuvomereza chiombolo cha madzi ndi Mzimu kuti aomboledwe. Angakhale olungama kokha kudzera mu chiombolo cha madzi ndi Mzimu.
Ndi uthenga wabodza kukakamira kuti tchimo loyamba lokha ndi lomwe linakhululukidwa mwa Yesu ndipo tiyenera kulapa machimo athu a tsiku ndi tsiku kuti tipeze chipulumutso. Ichi chidzatipitsa molunjika ku gehana. Choncho okhulupilira ambiri amadzipereka okha ku gehena mwa kukhulupilira uthenga wabodzawu ndipo khalidwe limeneli lafala kwambiri m’masiku oipa ano.
Kodi mungadziwe kuti mwagwera mu uthenga onama? Kodi mungakhalebe ongongola pamene munapereka ngongole zanu zonse? Ganizani pa zimenezi. Ngati mumaziona kuti ndinu ochimwa pamene mukukhulupilira mwa Yesu, kodi munganene kuti mukukhulupilira mwa Iye moyenera? Kodi ndinu okhulupilira komanso ochimwa, kapena ndinu okhulupilira ndiponso munthu olungama?
Mungasankhe nokha. Mungakhulupilire kuti machimo anu onse anakhululukidwa, kapena mungakhulupilire kuti mudzilapa masiku onse pa zolakwa zanu. Chisankho chanu chidzanena kuti muzapita Kumwamba kapena ku gehena. Muyenera kumvera ku mlaliki amene akukuuzani uthenga wabwino oona.
Iwo amene akhulupilira mu uthenga onama amapempherabe kuti akhululukidwe machimo pa msonkhano wa madzulo ulimonse, pa kukumana kwa tsiku lachitatu, tsiku lachisanu lili lonse pamapemphero a usiku-onse ndi cholinga kuti atsuke machimo awo.
“Ambuye, ndachimwa. Ndachimwa sabata lino,” amanena choncho. Ndiyeno amakumbukira machimo a zaka zapita ndi kupempheranso kuti awakhululukire. Uko ndi kuipitsa uthenga wabwino odalitsika wa kubadwanso mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.
Machimo athu ayenera kulipiridwa ndi mwazi. Ahebri 9:22 anena kuti, “Ndipo wopanda kukhetsa mwazi kulibe kumasuka.” Ngati muganiza kuti muli ndi uchimo, kodi ndiye kuti mukupempha Iye kuti akhetsenso mwazi kwa inu kobwereza? Iwo amene sakhulupilira mu chiombolo chonse ali ndi mlandu wa kutembenuza chiombolo cha Yesu kukhala chabodza. Iwo moona akukakamira kuti Yesu sanaombole ife kamodzi kokha ndiponso kuti Iye ndi onama.
Kuti tiomboledwe mwa Yesu, muyenera kukhulupilira mu choonadi cha chiombolo cha madzi ndi Mzimu. Kodi mungakhululukidwedi machimo ndi mazana, zikwi, mamiliyoni a mapemphero? Uthenga wabwino oona unaombola ife kamodzi kokha. Khalani olungama, pitani ku Ufumu wa Kumwamba, ndi kukhala ndi umoyo wolungama nthawi zonse.
“♪Ndikukhala moyo watsopano mwa Yesu. Kale lapita ndipo ndakhala cholengedwa chatsopano. Kale loipa lachoka. O, Yesu ndiye moyo wanga weniweni. Ndikukhala moyo watsopano mwa Yesu.♪”
Mukukhala moyo watsopano mwa Yesu. Zilibe kanthu kuti simukuoneka okongola m’mene mukufunira kukhalira, ngakhale ndinu wamfupi kwambiri, kapena onenepa kwambiri pakatikati, iwo amene anadalitsika ndi uthenga wabwino wakubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu akukhala ndi moyo osangalala. Kodi zili ndi phindu lotani kuti mphuno yanu ndiyosapangidwa bwino, kapena ndinu wamfupi pang’ono? Chifukwa sindife angwiro, tinapulumutsiwa mwa kukhulupilira mu kukhala obadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu mwa Yesu. Koma iwo amene akuziona kuti ndi ovomerezeka adzapezeka ku gehena.
Zikomo, Ambuye. Nthawi zonse ndimapereka chiyamiko kwa Ambuye. Chifukwa tikukhulupilira mu kubadwanso mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu, tidzalandiridwa Kumwamba.
KUPANDA CHOONADI KUDZATITENGERA KU GEHENA
Kodi ndi ndani adzalandira korona wa chilungamo pomaliza?
Iye amene wagonjetsa chabodza
Chabodza chikutiuza kuti tiyenera kulapa masiku onse kuti tikhululukidwe, koma uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ukutiuza kuti ndife okhululukiridwa kale ndipo chimene tiyenera kuchita ndi kungokhulupilira basi.
Kodi choonadi ndi chiti? Kodi tiyenera kulapa masiku onse? Kapena kodi ndi koyenera kukhulupilira kuti Yesu anaombola ife pamene anabatizidwa mu njira yoyenera koposa kuti achotse machimo athu? Choonadi ndi chakuti Yesu anachotsa machimo athu kamodzi kokha ndipo mu njira yabwino imeneyi anatipatsa chipulumutso.
Tiyenera kupambana pa chosalungama mu nkhondo yauzimu. Athu ambiri akutsatira chabodza. “Ndipo kwa mngeli wa mpingo wa ku pergamo lemba: Izi anena Iye wokhala nalo lupanga lakuthwa konse konse: Ndidziwa kumene ukhalako kuja kuli mpando wacifumu wa Satana; ndipo ugwira dzina langa, osakaniza cikhulupiriro canga, angakhale m’masiku a Antipa, mboni yanga, wokhulupirika wanga, amene anaphedwa pali inu, kuja akhalako satana.” (Chivumbulutso 2:12-13).
“Kwa iye wolakika, ndidzampatsa mana obisika, ndipo ndidzampatsa mwala woyera, ndi pa mwalawo dzina latsopano lolembedwapo, wosalidziwa munthu ali yense koma iye wakuulandira.” (Chivumbulutso 2:17).
Pamene mizimu yoipa yambiri yakhalamo ndipo chabodza chaima ndi kuonetsa ngati ndi choonadi, Satana amaonekera ngati m’ngelo onyezimira. Mulungu sangathandize aliyense amene akumva ndi kudziwa choonadi cha chipulumutso cha madzi ndi Mzimu koma sakukhulupilira chimenecho. Munthu otere adzapita ku gehena.
Aliyense ayenera kuganizira pa iye yekha kuti mwina akhulupilire mu chipulumutso cha Yesu. Palibe yemwe angagwade pamaso panu, kukuchondelerani kuti mukhulupilire ndi kukhala woomboledwa.
Ngati mufuna kuti mupulumutsidwe ku uchimo, ndiye khulupilirani mu chipulumutso cha madzi ndi Mzimu. Ngati mukumva kuyamika chifukwa cha chikondi chake mu chipulumutso ndi chisomo Chake mu kupulumutsa ife, ndiyeno khulupilirani. Ngati ndinu ochimwa oyenera kupita kugehena, ndiyeno khulupilirani mu madzi ndi mu Mzimu, ubatizo wa Yesu ndi imfa Yake ya pa Mtanda. Ndiye kuti muzakhala olungama.
Ngati muganiza kuti sindinu ochimwa, simuyenera kuomboledwa mwa kukhulupilira mwa Yesu. Ochimwa okha ndi amene aomboledwa ku machimo awo mwa kukhulupilira mu uthenga wabwino wakubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Yesu ndi Mpulumutsi wa ochimwa ndi odzudzula wa ovutika. Iye ndi Mlengi. Iye ndi Mbuye wa Chikondi.
Ndikukupemphani kuti mukhulupilire mu uthenga wabwino wa kubadwanso mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Khulupilirani m’menemo. Mudzakhala okhulupilira kuti Yesu ndi Mpulumutsi, Mzathu, Mbusa ndi Mulungu kwa inu. Ochimwa ayenera kukhulupilira mwa Yesu. Ngati simukufuna kupezeka ku gehena, muyenera kukhulupilira m’menemo. Mulungu sakutichonderera kuti tikhulupilire mu uthenga wabwino wa chipulumutso.
Kodi mukufuna kukakhala Kumwamba? Ndiyeno khulupilirani mu uthenga wabwino wa kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Yesu anati, “Ine ndine njira, choonadi, ndi moyo. Khulupilirani mwa Ine.” Kodi mukunena kuti mukufuna kuponyedwa mu gehena? Ndiyeno musakhulupilire. Iye akuti wakonzeratu malo mu gehena a inu.
Mulungu samachondelera. Wa zamalonda amalandira anthu alionse kuti agulitse zinthu zake, koma Mulungu amapereka Ufumu wa Kumwamba kwaulere kwa iwo okha amene ndi oomboledwa. Mulungu ndi chilungamo.
Anthu akunena kuti kutha kwa dziko kuli pafupi. Inde, inenso ndikuganiza choncho. Ndipo ndi kupusa kusakhulupilira mu uthenga wabwino weniweni wa kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.
Khulupilirani mu chipulumutso cha uthenga wabwino odalitsika wakubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Tiyeni tipite limodzi ku Ufumu wa Kumwamba. Kodi simudzapita ndi ine kumalo abwino okhala Yesu?
Kodi ndinu ochimwa kapena munthu olungama?
Munthu olungama amene alibe uchimo mu mtima mwake
Tiyeni tiwerenge kuchokera pa Aroma 8:1-2 “Cifukwa cace tsopano iwo akukhala mwa Kristu Yesu alibe kutsutsidwa. Pakuti cilamulo ca mzimu wa moyo mwa Kristu Yesu candimasula ine ku lamulo la ucimo ndi la imfa.”
Yesu anachotsa machimo athu onse kudzera mu ubatizo Wake komanso imfa Yake ya pa Mtanda. Iye anapulumutsa ochimwa onse amene anayenera kuweruzidwa chifukwa cha machimo awo.
Chipulumutso cha Mulungu chili ndi zinthu ziwiri. Chimodzi ndi lamulo ndipo china ndi Chikondi Chake. Lamulo likutiphunzitsa kuti ndife ochimwa. Mogwirizana ndi lamulo, mphotho yauchimo ndi imfa. Sitingapulumutsidwe mwa lamulo. Limangotiphunzitsa za khalidwe lathu lauchimo ndi kulakwa kwathu. Likutidziwitsa kuti ndife ochimwa.
Kuti alipire mphotho yauchimo, Yesu anadza ku dzikoli kudzachotsa machimo athu onse ndi kuwalipira iwo ndi moyo Wake kuti apulumutse ife ku chiweruzo. Ndi chikondi cha Mulungu chimene chinapulumutsa ife ku uchimo onse.
Tiyenera kupambana ku chabodza. Mulungu amapereka dalitso la kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu kwa aja amene akugonjetsa chabodza.
Tinapulumutsidwa mwa kukhulupilira mwa Yesu. Mwa kukhulupilira m’mawu Ake, timapeza chilungamo ndi kumvetsetsa choonadi. Khulupilirani mu choonadi cha kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu mu mitima yanu, ndipo mudzapulumutsidwa.