(Ahebri 7:1-28)“Pakuti Melikizedeke uyu, Mfumu ya Salemu, wansembe wa Mulungu Wamkulukulu, amene anakomana ndi Abrahamu, pobwera iye adawapha mafumu aja, namdalitsa, amenenso Abrahamu anamgawira limodzi la magawo khumi la zonse (ndiye posandulika, poyamba ali Mfumu ya cilungamo, pameneponso Mfumu ya Salemu, ndiko, Mfumu ya mtendere; wopanda atate wace, wopanda amace, wopanda mawerengedwe a cibadwidwe cace, alibe ciyambi ca masiku ace kapena citsiriziro ca moyo wace, wofanizidwa ndi Mwana wa Mulungu), iyeyu wakhala wansembe kosalekeza. Koma tapenyani ukulu wake wa iyeyu, amene Abrahamu, kholo lalikuru, anampatsa limodzi la magawo khumi la zosankhika za kunkhondo. Ndipo iwotu mwa ana a Levi akulandira nchito yakupereka nsembe, ali nalo lamulo lakuti atenge limodzi la magawo khumi kwa anthu monga mwa cilamulo, ndiko kwa abale ao, angakhale adaturuka m’cuuno ca Abrahamu; koma iye amene mawerengedwe a cibadwidwe cace sacokera mwa iwo, anatenga limodzi la magawo khumi kwa Abrahamu, namdalitsa iye amene ali nao malonjezano. Ndipo popanda citsutsano konse wamng’ono adalitsidwa ndi wamkuru. Ndipo pano anthu ofeka alandira limodzi la magawo khumi; koma apo iye, woti adamcitira umboni ali ndi moyo. Ndipo kuli ngati kunena, mwa Abrahamu Levinso wakulandira limodzi limodzi la magawo khumi; pakuti pajapo anali m’cuuno ca atate wace, pamene Melikizedeke anakomana naye. Ndipo pakadakhala ungwiro mwa unsembe wa Cilevi (pakuti momwemo anthu analandira cilamulo), pakadatsala kusowa kotani kuti auke wansembe wina monga mwa dongosolo la Melikizedeke, wosayesedwa monga mwa dongosolo la Aroni? Pakuti posandulika unsembe, kufunikanso kuti lamulo lisandulike. Pakuti iye amene izi zineneka za Iye, akhala wa pfuko lina, wa ili palibe munthu watumikira guwa la nsembe. Pakuti kwadziwikandi kuti Ambuye wathu anaturuka mwa Yuda; za pfuko ili Mose sanalankhula kanthu ka ansembe. Ndipo kwadziwikatu koposa nditu, ngati auka wansembe wina monga mwa mafanidwe a Melikizedeke, amene wakhala si monga mwa lamulo la lamuliro la kwa thupi, komatu monga mwa mpambvu ya moyo wosaonongeka; pakuti amcitira umboni, Iwe ndiwe wansembe nthawi yosatha Monga mwa dongosolo la Melikizedeke. Pakuti kuli kutaya kwace kwa lamulo lidzadza kalelo, cifukwa ca kufoka kwace, ndi kusapindulitsa kwace (pakuti cilamulo sicinacitira kanthu kakhale kopanda cirema), ndipo kulinso kulowa naco ciyembekezo coposa, cimene tiyandikira naco kwa Mulungu. Ndipo monga momwe sikudacitika kopanda lumbiro; (pakuti iwotu anayesedwa ansembe kopanda lumbiro; koma Iye ndi lumbiro mwa Iye amene ananena kwa Iye, walumbira Ambuye ndipo sadzalapa, Iwe ndiwe wansembe nthawi yosatha). Momwemonso Yesu wakhala Nkhoswe ya pangano loposa. Ndipo iwo ndiwo ambiri anakhala ansembe, popeza imfa idawaletsa asakhalebe; koma Iye cifukwa kuti akhala Iye nthawi yosatha ali nao unsembe wosasinthika, kucokera komweko akhoza kupulumutsa konse konse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nao moyo wace cikhalire wa kuwapembezera iwo. Pakuti mkulu wa nsembe wotere anatiyenera ife, woyera mtima, wopanda coipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ocimwa, wakukhala wopitirira miyamba; amene alibe cifukwa ca kupereka nsembe tsiku ndi tsiku monga akulu a nsembe, yoyambira cifukwa ca zoipa za anthu; pakuti ici anacita kamodzi, kwatha, podzipereka yekha. Pakuti cilamulo cimaika akuru a ansembe anthu, okhala naco cifoko; koma mau a lumbirolo, amene anafika citapita cilamulo, aike Mwana, woyesedwa wopanda cirema ku nthawi zonse.”
YESU ANATUMIKIRA UNSEMBE WA KUMWAMBA
Kodi ndi ndani wamkulu, wansembe wamkulu Melekizedeke kapena wamkulu wansembe wadziko wa mbaja la Aroni?
Wansembe wamkulu Melekizedeki
Mu Chipangano Chakale, munali wamkulu wansembe otchedwa Melekizedeke. Mu nthawi ya Abrahamu, Kedorelaomere ndi mafumu ena anagwirizana pamodzi, kunyamula katundu onse wa Sodomu ndi Gomora. Abrahamu anapita kunkhondo ndi atumiki ake ophunzitsidwa bwino, amene anabadwa m’nyumba yake, ndi kuwatsogolera ku nkhondo kukamenyana ndi Kedorelaomere ndi asilikali ake.
Kumeneko, anagonjetsa Kedorelaomere, mfumu ya ku Elamu, pamodzi ndi asilikali a mafumu amene anagwirizana nao aja ndi kubweretsa mchimwene wake Loti ndi katundu wake. Pamene Abrahamu anabwerera kuchokera mu kugonjetsa adani ake, Melekizedeki, Mfumu yaku Salemu ndi wansembe wa Mulungu Wamkulu kwambiri, anabweretsa mkate ndi vinyo ndi kudalitsa nawo Abrahamu. Ndipo Abrahamu anamupatsa chakhumi cha zonse (Genesis 14).
Mbaibulo, ukulu wa wansembe wamkulu Melekizedeki ndi akulu a ansembe m’ndondomeko yake unafotokozedwa mwatsatanetsatane. wamkulu Wansembe Melekizedeki anali “mfumu yamtendere,” “mfumu wachilungamo,” opanda atate, opanda amai, opanda kochokera. Alibe kuyamba kwamasiku kapena kutha kwa moyo, koma anapangidwa ngati Mwana wa Mulungu, anakhalabe wansembe mopitilira.
Baibulo limatiuza kuti tiganizire mwanzeru ukulu wa Yesu Kristu, amene anali wamkulu wansembe wa ndondomeko ya Melekizedeke, mwa kusiyanitsa unsembe wa Yesu wa mu Chipangano Chatsopano ndi uja wansembe wamkulu Aroni wa mu Chipangano Chakale.
Mbadwa za Levi zinakhala ansembe ndi kumatenga chakhumi kwa anthu, icho chinali, cha abale awo, ngakhale kuti anali mbadwa za Abrahamu. Koma pamene Abrahamu anali kupereka chakhumi kwa wamkulu wansembe Melekizedeke, Levi anali adakali mchiuno mwa atate ake.
Kodi ansembe a mu Chipangano Chakale anali aakulu koposa Yesu? Zinafotokozedwa mu Baibulo. Kodi Yesu anali wamkulu kuposa ansembe a padziko lapansi? Kodi ndani angadalitsidwe ndi wina? Olemba buku la Ahebri ananenapo za ichi kuyambira pachiyambi. “Ndipo popanda citsutsano konse wamng’ono adalitsidwa ndi wamkuru” Abrahamu anadalitsidwa kudzera mwa wamkulu wansembe Melekizedeke.
Kodi tizakhala bwanji mu chikhulupiliro chathu? Kodi tidalire mu malamulo a Mulungu kudzera mu ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe ya pa chihema choyera ya mu Chipangano Chakale, kapena tidalire pa Yesu Kristu amene anabwera kwa ife ngati wamkulu wansembe wakumwamba kudzera mu nsembe yake ya madzi ndi Mzimu?
Kulingana ndi katanthauzidwe kake kamene tingasankhe, ndife odalitsika kapena owonongedwa. Kodi tikukhala mogwirizana ndi mawu a Mulungu ndi kupereka nsembe masiku onse, kapena tikusankha kuti tikhulupilire mu chipulumutso chimene Yesu anapereka kwa ife mwa kuzipereka Yekha nsembe kamodzi kokha ndi madzi komanso mwazi? Tiyenera kusankha chimodzi pa izi ziwiri.
Mu masiku a Chipangano Chakale, anthu a Israyeli ankayang’ana kwa mbumba ya Aroni ndi Levi. Mu masiku a mu Chipangano Chatsopano, ngati tafunsidwa kuti wamkulu ndani, Yesu kapena ansembe a ndondomeko ya Aroni? Ndiyeno, popanda kufunsa, tingayankhe kuti ndi Yesu amene ndi wamkulu. Koma pamene anthu akudziwa choona chimenechi bwino, ochepa okha ndi amene akutsatira m’chikhulupiliro chawo.
Baibulo limatipatsa yankho lokwanira la funso limeneli. Ikutiuza kuti Yesu, amene anali wa mtundu osiyana kumene palibe amene anapulumutsidwa pa guwa, anatenga unsembe wakumwamba. “Pakuti posandulika unsembe, kufunikanso kuti lamulo lisandulike.”
Mulungu anapatsa anthu a ku Israyeli malamulo ndiponso ndime zokwanira 613 za Chilamulo kudzera mwa Mose. Mose anauza anthu kuti akhale mogwirizana ndi lamulo komanso malamulo, ndipo anthu anavomereza kuchita zimenezo.
Kodi chifukwa n’chiyani Mulungu anaika pambali pangano loyamba ndi kukhazikitsa lachiwiri?
Chifukwa chakuti munthu anali ofoka kwambiri kuti akhale ndi moyo mogwirizana ndi pangano loyamba.
Mbaibulo, Anthu a ku Israyeli analumbira kuti adzakhala m’malamulo a Mulungu pa mabuku oyamba: Genesis, Ekisodo, Levitiko, Numeri, ndi Deuteronomo. Mulungu ananenera lamulo lililonse kwa iwo ndipo anati, “Inde” ku lamulo lililonse popanda kukaika.
Komabe, tingaone kuti pambuyo pa Deuteronomo, kuyambira pa Yoswa kupita kutsogolo, sanakhale molingana ndi malamulo a Mulungu. Kuchokera pa Oweruza kufikira ku Mafumu oyamba ndi mafumu wachiwiri, anayamba kuukira atsogoleri awo, ndipo kuchoka pamenepo, anavunda kwambiri moti anasintha ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe pa chihema.
Ndipo pomaliza mu Malaki, anabweretsa nyama zosayenera kuperekedwa mosemphana ndi lamulo la Mulungu lopereka nyamba zimene zilibe chilema. Iwo anafunsa wansembe, “Chonde osapenya imeneyi. Chonde vomerani imeneyi.” M’malo mopereka nsembe kulingana ndi lamulo la Mulungu, anasintha mosayembekezereka.
Anthu a ku Israyeli sanasunge lamulo la Mulungu kwanthunthu ngakhale kamodzi mu nthawi ya Chipangano Chakale. Iwo anaiwala ndi kunyalanyaza chipulumutso chinabvumbulutsidwa m’ndondomeko. Motero Mulungu anayenera kusintha ndondomeko yoperekera nsembe. Mu Yeremiya, Mulungu anati, “ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israyeli, ndi nyumba ya Yuda.”
Tiyeni tione pa Yeremiya 31:31-34. “Taonani, masiku adza, ati Yehova, ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israyeli, ndi nyumba ya Yuda; si monga pangano limene ndinapangana ndi makolo ao tsiku lija ndinawagwira manja kuwaturutsa m’dziko la Aigupto; pangano langa limenelo analiswa, ngakhale ndinali mbuyao, ati Yehova. Koma ili ndi pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Israyeli atapita masiku aja, ati Yehova; ndidzaika cilamulo canga m’kati mwao, ndipo m’mtima mwa ndidzacilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, nadzakhala iwo anthu anga; ndipo sadzaphunzitsa yense mnansi wace, ndi yense mbale wace, kuti, mudziwe Yehova; pakuti iwo onse adzandidziwa, kuyambira wamng’ono kufikira wamkuru wa iwo, ati Yehova; pakuti ndidzakhululukira mphulupulu yao, ndipo sindidzakumbukira cimo lao.”
Mulungu anati adzapanga pangano latsopano. Iye anapanga kale pangano ndi anthu a Israyeli, koma analephera kukhala mwa mawu a Mulungu. Mwa ichi, anagnaiza zopanga pangano latsopano la chipulumutso ndi anthu Ake.
Iwo analumbira pamaso pa Mulungu, “Tizalambira Inu nokha ndi kukhala mwa mawu Anu ndi malamulo.” Mulungu anawauza iwo, “Musakhale ndi milungu ina koma Ine ndekha,” ndipo anthu a ku Israeli anati, “Inde, sitizalambira mulungu wina. Inu ndi Mulungu Yekha wa ife. Sikungakhale mulungu wina kwa ife. Koma analephera kusunga lumbiro lawo.
Gwero la lamulo ndi Malamulo Khumi: Musakhale ndi milungu ina koma Ine ndekha. Musazipangire nokha fano losema kapena chifaniziro, kapena chilichonse cholingana ndi chinachake ndi kuchigwadira kapena kuchirambila. Muzikumbukira tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika. Musatenge dzina la Ambuye Mulungu wanu pachabe. Lemekezani atate anu ndi amai anu. Musaphe. Musachite chigololo. Musabe. Musachitire umboni onama kwa mnansi wanu. Musasilire nyumba ya mnansi wanu” (Ekisodo chaputala 20).
Ndiponso adzigawa mu ndime zokwanira 613 amene anayenera kusungidwa pa umoyo wawo onse. “Chimene sichifunika kuchitika ku ana akazi, ndi chimene sichiyenera kuchitika ku ana amuna, zimene ziyenera kuchitika ku amai opeza….” Lamulo la Mulungu linawalamula kuchita zinthu zonse zabwino ndipo asachite chilichonse choipa. Awa ndi malamulo khumi ndi ndime za tsatanetsatane zokwanira 613.
Komabe, mwa mtundu wa anthu onse, panalibe ndi m’modzi yemwe amene anatha kusunga ndime zonse za lamulo Lake. Motero Mulungu anayenera kuganizira njira ina ya iwo kuti apulumutsidwe ku machimo awo onse.
Kodi unsembe unasintha liti? Pamene Yesu anabwera pa dziko lapansi, unsembe unasinthidwa. Yesu ananyamula unsembe kwa ansembe onse a ndondomeko ya Aroni. Anaika pambali nsembe za pa chihema zimene zinali ndi mwambo wa kulowetsa unsembe wa ndondomeko ya Levi. Iye Yekha anatumikira unsembe wa kumwamba.
Iye anabwera ku dziko lapansili, osati ngati mbadwa ya Aroni, koma ngati mbadwa ya Yuda, nyumba ya mafumu. Anazipereka Yekha ngati nsembe kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi wa pa Mtanda ndi kupulumutsa mtundu onse wa anthu ku machimo awo.
Mwa kuzipereka Yekha, anakwanitsa kuti ife tikonze vuto la uchimo. Iye anatsuka machimo onse a mtundu wa anthu kudzera mu nsembe ya ubatizo ndi mwazi. Iye anapereka nthawi imodzi nsembe yosatha ya uchimo onse.
KUSINTHA KWA UNSEMBE KUNALINSO NDI KUSINTHA PAMODZI KWA CHILAMULO
Kodi lamulo losinthidwa lachipulumutso ndi chiyani?
Nsembe imodzi yosatha ya Yesu Kristu
Okondedwa abwenzi, unsembe wa mu Chipangano Chakale unasinthidwa mu Chipangano Chatsopano. M’masiku a Chipangano Chakale, wamkulu wansembe mwa mbumba ya Aroni, wa m’nyumba ya Levi, anali kupereka nsembe kuti atetezere machimo a Israyeli m’zaka zapitazo. Wamkulu Wansembe anali kulowa mu malo Oyeretsetsa. Anali kupita pamaso pa mpando wachifundo ndi mwazi wa nyama yoperekera nsembe. Wansembe yekha ndi amene anali kutha kupita kutsogolo kwa chinsaru chotchinga, kumene kunali malo Oyeretsetsa.
Koma Yesu atabwera, unsembe wa Aroni unaperekedwa kwa Iye. Yesu ananyamula unsembe osatha. Iye anatumikira unsembe wamuyaya mwa kuzipereka yekha, kuti mtundu onse wa anthu upulumutsidwe ku machimo awo onse.
M’Chipangano Chakale, wamkulu wansembe ankayeneranso kutetezera machimo ake mwa kuika manja pamutu pa ng’ombe asanatumikire anthu ake onse. Ankapereka machimo ake ma kuika manja, ndi kunena kuti, “Mulungu, ndachimwa.” Ndiyeno ankapha nyamayo ndi kuwaza mwazi wake kutsogolo kwa mpando wachifundo kasanu ndi kawiri.
Ngati wamkulu wansembe Aroni iye mwini anali operewera, mungaganizire m’mene anthu analili odwala. Mwana wa Levi, wamkulu wansembe Aroni iyenso anali ochimwa. Choncho anayenera kupereka ng’ombe yamphongo kuti atetezere machimo a iye yekha ndi aja a banja lake.
Ambuye ananena kuti mu Yeremiya mndime ya 31, “Ndizaphwanya pangano. Ndanapanga pangano ndi inu, koma simunalisunge. Motero Ndizaika pambali pangano limene silinakuyeretseni ndi kukupatsani pangano la tsopano la chipulumutso. Sindizakupulumutsaninso kudzera mu malamulo Anga, koma m’malo mwake kukupatsani chipulumutso kudzera mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.”
Mulungu anatipatsa pangano latsopano. Pamene nthawi inabwera, Yesu anabwera kudziko lapansili mu kulingana ndi munthu, anadzipereka yekha kuti anyamule machimo a dziko lapansi ndi kukhetsa, mwazi pa Mtanda ndi kuchotsa machimo kuti apulumutse tonse amene tikukhulupilira mwa Iye. Anachotsa machimo onse a mtundu wa anthu kudzera mu ubatizo wake.
Lamulo la Mulungu linaikidwa pambali ndipo linasinthidwa. Anthu a Israyeli akanapulumutsidwa akanakhala kuti anachita mogwirizana ndi lamulo la Mulungu, koma analephera kuchita zimenezo.“Pakuti ucimo udziwika ndi lamulo” (Aroma 3:20).
Mulungu ankafuna Aisyraeli kuzindikira kuti anali ochimwa ndiponso kuti lamulo silikanawapulumutsa iwo. Iye anawapulumutsa kudzera mu lamulo lachipulumutso la madzi ndi Mzimu, osati kudzera mu ntchito zawo. Mu chikondi Chake chosatha, Mulungu anatipatsa pangano latsopano m’mene tingapulumukire ku machimo onse a dziko kudzera mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu.
Ngati mukhulupilira mwa Yesu popanda kudziwa tanthauzo la ubatizo Wake ndi mwazi, chikhulupiliro chanu chonse ndi cha chabe. Pamene mukuchita choncho, muli ovutika kwambiri kuposa pamene simunkakhulupilira mwa Yesu.
Mulungu ananena kuti anayenera kupanga pangano latsopano kuti apulumutse mtundu wa anthu ku machimo awo. Mwa ichi, tsopano ndife opulumutsidwa osati mwa lamulo la ntchito zathu, koma mwalamulo la chilungamo la chipulumutso kudzera mu madzi ndi mwazi.
Iyi inali lonjezo Lake losatha ndipo Iye anakwaniritsa lonjezo Lake kwa ife amene tikhulupilira mwa Yesu. Ndipo anatiuza za ukulu wa Yesu. Anatiuza m’mene alili wamkulu mwa kusiyanitsa Iye ndi ansembe a ndondomeko ya Aroni mu Chipangano Chakale.
Timakhala oyenera mwa kukhulupilira mu chipulumutso kudzera mu madzi ndi mwazi wa Yesu. Chonde ganizirani chimenechi mwanzeru. Zilibe kanthu kuti m’busa wanu anaphunzira kapena akunena bwino motani, kodi angakhale bwanji opambana Yesu? Kulibe njira iliyonse. Tingapulumutsidwe kudzera kokha mu uthenga wabwino wa madzi ndi mwazi, osati kumvera chabe malamulo a Mulungu. Chifukwa unsembe unasinthidwa, lamulo la chipulumutso nalonso linasinthidwa.
KUPAMBANA KWA CHIKONDI CHA MULUNGU
Kodi chopambana ndichiti, chikondi cha Mulungu kapena lamulo la Mulungu?
Chikondi cha Mulungu
Tingapulumutsidwe pokhapo ngati tikukhulupilira mwa Yesu, podziwa m’mene Yesu anapulumutsira ife ndiponso m’mene kukula kwa chikondi Chake chilili kwa ife. Ndiyeno, kodi kusiyana kuli pati pakati pa chikhulupiliro mu malamulo ndi chikhulupiliro mu ukulu wa chikondi cha Mulungu?
Akatswiri azamalamulo amalemerera kwambiri kufunika kwa ziphunzitso zawo zachipembezo ndi ukatswiri waumwini koposa mawu a Mulungu. Komabe, choona ndiponso chikhulupiliro chanthunthu chauzimu mwa Yesu chimabwera mwa khulupilira mu ukulu wa chipulumutso chinakwaniritsidwa kudzera mwa madzi ndi Mzimu.
Ngakhale lero, anthu ambiri amanena kuti tchimo loyamba linakhululukidwa, koma ayenera kulapa masiku onse chifukwa cha machimo awo atsiku ndi tsiku. Anthu ambiri amakhulupilira zimenezi ndi kuyesa kukhala ndi miyoyo yawo mogwirizana ndi malamulo a mu Chipangano Chakale. Iwo sanadziwebe za kupambana kwa chipulumutso cha Yesu chimene chinabwera mwa madzi ndi Mzimu.
Mu Chipangano Chakale, Israyeli anayenera kukhala mwa lamulo la Mulungu kuti apulumutsidwe ku machimo awo, koma sanapulumutsidwe. Chifukwa chakuti Ambuye akudziwa kufoka kwathu komanso choona chakuti ndife operewera, Iye anaika pambali lamulo Lake. Sitingapulumutsidwe kudzera mu ntchito zathu zokha. Yesu anati adzatipulumutsa kudzera mu uthenga Wake wabwino wa madzi ndi Mzimu. Iye anati, “Ndizakuombolani nonse ku machimo anu pa Ine ndekha.” Mulungu analosera zimenezo mu Genesis.
“ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yace; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira citende cace.” (Genesis 3:15). Pambuyo pakuti Adamu ndi Eva achimwa ndi kugwa, anasoka masamba a mtengo wa mkuyu ngati matewera kuti abise uchimo wawo kwa Mulungu. Koma Mulungu anawaitana ndi kupanga matewera kuchokera ku zikopa za nyama ngati chizindikiro cha chipulumutso. Genesis akunena za mitundu iwiri ya matewera a chipulumutso. limodzi linapangidwa kuchokera ku masamba a mkuyu, ndipo linalo linapangidwa kuchoka ku chikopa. Kodi muganiza kuti thewera labwino ndi liti? Indedi, matewera a zikopa ndi abwino chifukwa moyo wa nyama unaperekedwa kuti upulumutse munthu.
Matewera a masamba a mkuyu akananyala mwamsanga. Munga mukudziwa kale, tsamba la mkuyu limaoneka ngati dzanja lomwe lili ndi zala zisanu. Choncho, kuvala thewera la masamba a mtengo wa mkuyu kukutanthauza kubisa machimo a munthu kumbuyo kwa zinthu zabwino. Ngati mungavale thewera la masamba a mtengo wa mkuyu ndi kukhala pansi, masamba angang’ambike mosachedwa kukhala zidutswa. Ndinkakonda kupanga zida kuchoka ku masamba a mtengo kupanga masewera a usilikali pamene ndinali mwana. Koma zilibe kanthu kuti ndinali kuvala mochenjera motani, zinkang’ambika potha kwa tsiku. Mnjira imodzimodzi, mtundu wa anthu wathupi lovunda lapangitsa kuti chiyeretso chisatheke.
Koma chipulumutso cha madzi ndi mwazi, ubatizo wa Yesu ndi imfa Yake ya pa Mtanda yapulumutsa kwathunthu ochimwa ambiri kuti anenere ukulu wa chikondi cha Mulungu. Umo ndi m’mene kupambana kwa chikondi cha Mulungu chilili ku lamulo la Mulungu.
AJA AMENE ALI NDI CHIKHULUPILIROBE MU LAMULO LA MULUNGU
Kodi n’chifukwa chiyani akatswiri azamalamulo amapanga zovala zatsopano za nchito yawo ya masiku onse?
Chifukwa chakuti sakudziwa kuti nchito zawo sizingawapangitse kukhala olungama.
Iwo amene akupanga matewera awo ndi masamba a mtengo wa mkuyu akukhala moyo wawo mwalamulo. Okhulupilira osocherawa ayenera kusintha matewera awo nthawi zonse. Ayenera kupanga matewera atsopano nthawi iliyonse pamene akupita ku mpingo patsiku lamulungu. “Okondedwa Mulungu, Ndinachimwa kwambiri mlungu watha. Koma Ambuye, ndinakhulupilira kuti munandipulumutsa pa Mtanda. Ambuye, chonde tsukani machimo anga ndi mwazi wa pa Mtanda!” Amasoka matewera atsopano pomwepo. “Oho, tamandani Ambuye. Aleluya!”
Koma posachedwa adzayenera kusokanso matewera ena ku nyumba. Chifukwa chiyani? Chifukwa akale aja ang’ambika. “Okondedwa Ambuye, ndachimwanso masiku atatu apitawa. Chonde ndikhululukireni.” Amapanga ndi kuvala matewera atsopano a kulapa mobwereza bwereza.
Pachiyambi, matewera angakhaleko masiku ambiri, koma popita panthawi, amafuna atsopano. Popeza sakanatha kukhala mwa lamulo la Mulungu, amakhala amanyazi pa iwo okha. “Oho, ichi ndi chochititsa manyazi bwanji. Ambuye, oho, Ambuye, Ndachimwanso kachiwiri!” Ndipo ayenera kupanga matewera atsopano a kulapa. “Oho, Ambuye, ndikovuta kupanga zovala za mtengo wa mkuyu tsiku la lero.” Amagwira ntchito yaikulu kuti asoke matewera atsopano.
Pamene anthu otere aitana pa Ambuye, ndiye kuti ndi kuulula machimo awo. Amaluma milomo yawo ndi kuitanira kwa Mulungu, “Mulu~ngu!” ndikupitiliza kupanga matewera atsopano masiku onse, Ndiyeno, chimachitika ndi chiyani pamene atopa kuchita choncho?
Kamodzi kapena kawiri pa chaka, amapita ku mapiri ndi kusala kudya. Amayesa ndi kupanga molimbika matewera-olimba. “Ambuye, chonde tsukani machimo anga. Chonde ndipangeni watsopano. Ndikhulupilira mwa Inu, Ambuye.” Amaganiza kuti ndi bwino kupemphera usiku. Choncho, amapumula nthawi yamasana ndipo pamene mdima ukuyandikira, amakangamira ku mitengo ndi mphamvu zawo zonse, kapena kupita ku mapanga ndi kulilira kwa Mulungu. “Ambuye, Ndikhulupilira mwa inu!” “♪Ndikulapa ndi kudzadza mtima wanga ndi maganizo achisoni♪” Amapemphera mofuula ndi kubangula, “Ndikhulupilira,” Mwa njira imeneyi amapanga matewera apadera amene amayembekezera kuti adzatenga nthawi, koma sizikhala choncho.
Ndi kotsitsimula chotani kutsika pa phiri pambuyo pa mapemphero! Monga kamphepo kotsitsimula, kapena mvula yamawawa yowazira pa mitengo ndi maluwa, miyoyo yawo ndi yodzala ndi mtendere ndiponso chisomo cha Wamphmvu yonse. Kumva oyera koposa mzimu wa ku phiri, amakumana ndi dziko atavala matewera apadera atsopano.
Koma akangobwerera ku nyumba zawo ndi kumpingo, ndi kuyamba kukhalanso, matewera amayamba kuda ndi kuyamba kung’ambika.
Abwenzi awo amafunsa, “Munali kuti?”
“Chabwino, ndinachokapo kwa kanthawi.”
“Mukuoneka ngati mwataya mphamvu!”
“Chabwino, inde, koma iyo ndi nkhani ina.”
Sangaulule kuti anali kusala chakudya, amapita ku mpingo kokha kukapemphera. “Sindizalakalaka akazi. Sindizanena bodza. Sindizasilira nyumba ya mnasi wanga. Ndizakonda anthu onse.”
Koma akangoona mkazi okongola wa miyendo yoonda bwino, kuyera kwa mitima yawo kumasintha pomwepo n’kukhala ndi chilakolako chenicheni. “Taonani m’mene siketi ija ilili yaifupi! Masiketi akungofupikirabe! Ndikuyenera kuonanso miyendo ija mobwereza! Oho! Ai! Oho, Ambuye! Ndachimwanso!”
Akatswiri azamalamulo amoneka opembedza, Koma muyenera kudziwa kuti ayenera kupanga matewera atsopano masiku onse. Chilamulo ndi chikhulupiliro cha m’matewera a masamba a mtengo wa mkuyu, chikhulupiliro cholakwika. Anthu ambiri amayesa kwambiri kukhala achipembezo mogwirizana ndi lamulo la Mulungu. Amafuula pamwamba pa mapapu awo pa mapiri kotero kuti mawu awo ayambe kumveka opembedza.
Akatswiri azamalamulo amagwira ntchito yofunikira pamene akutsogolera msonkhano wa mapemphero ku mpingo. “Atate Oyera wa Kumwamba! Tachimwa mlungu wapitawu. Chonde tikhululukireni…” Amachotsa misozi ndipo mpingo onse umatsatira. Iwo maganiza paokha kuti, wakhala nthawi yaitali ali kuphiri kupemphera ndi kusala chakudya. Akumveka wachipembezo ndiponso okhulupilika.” Koma chifukwa chakuti chikhulupiliro ndi cha chilamulo, ngakhale pamene mapemphero awo asanathe, mtima wa achilamulo umayamba kudzala ndi kuzikuza komanso uchimo.
Pamene anthu akupanga matewera atsopano apadera a masamba a mtengo wa mkuyu, nthawi zina angathe patapita miyezi iwiri kapena itatu. Koma posachedwa kapena patsogolo pang’ono, matewera amayamba kuchititsa manyazi ndipo amafunika kupanganso matewera atsopano ndi kupitiliza kukhala ndi moyo wawo wachinyengo. Uwu ndi moyo wa achilamulo umene akuyesa kukhala mwa lamulo kuti athe kupulumutsidwa. Ayenera kupitiliza kupanga matewera a tsopano kuchoka ku masamba a mtengo wa mkuyu.
Chilamulo ndi chikhulupiliro cha masamba a mkuyu. Akatswiri azamalamulo amakuuzani inu, “nonse munachimwa mlungu watha, kodi simunatero? Ndiyeno, lapani.”
Amakufuulirani ndi mawu okwera. “Lapani! Pempherani!”
Katswiri wa zamalamulo amadziwa m’mene angapangire mawu ake kumveka oyera. “Ambuye! Ndikupepesa. Sindinakhale mwa lamulo. Sindinasunge malamulo Anu. Ndikhululukireni Ambuye, ndikhululukireni kamodzinso.”
Sangakhale mwa lamulo ngakhale kuti amayesa molimbika kuchita choncho. Zoona zake, akuukira lamulo la Mulungu ndiponso Mulungu Yemwe. Iwo ndi amwano pamaso pa Mulungu.
ZOKONDA ZA CHUDAL BAY
Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu anaika padera lamulo?
Chifukwa chakuti linali lopanda ntchito kutipulumutsa ku uchimo.
Panali munthu wachichepere otchedwa Chudal Bay. Mu 1950, m’nthawi ya nkhondo ya ku Koriya, asilikali a chi kominisi anabwera ndi kulamula iye kuti asese malo pa tsiku la Sabata kuti amubele chikhulupiliro chake chaluntha ndi kum’panga kukhala mukominisi. Koma munthu wachipembezo wachichepereyu anakana kumvera malamulo awo. Anakakamira, koma munthu wachichepereyu anakananso.
Pomaliza, asilikali anamumangilira ku mtengo ndi kumuloza mfuti. “Ndi chiyani chimene ukufuna, kusesa malo onse kapena kuphedwa?”
Pamene anali kumukakamiza kuti apange chosankha, iye anati, “ndingafune kufa koposa kugwira ntchito patsiku la Sabata.”
“Wapanga chosankha chako, choncho tizakhala okondwa kugwirizana nawe.”
Mwamsanga anamuphulisa ndi kufa. Posachedwa, atsogoleri a mpingo anamusankha kukhala Dikoni atamwalira pofuna kukumbukira chikhulupiliro chake chosagwedera.
Ngakhale kuti anali ndi chifuno cha mphamvu, chikhulupiliro cha chipembezo chake chinasocheretsedwa. Kodi chifukwa chiyani sanasese malo onse ndi kulalikira uthenga wabwino kwa asilikali aja? Kodi n’chifukwa chiyani anali ouma mtima ndi kuufera? Kodi Mulungu azamutamanda chifukwa cha kusagwira ntchito pa tsiku la Sabata? Ai,
Tiyenera kukhala ndi moyo wauzimu. Osati zochita zathu koma chikhulupiliro chathu ndi chofunikira pamaso pa Mulungu. Atsogoleri a mpingo amafuna kukondwerera munthu ngati Chudal Bay chifukwa amafuna kuonetsa ukulu ndiponso chilolezo cha chipembezo chawo. Ali ngati Afalisi onyenga amene anaukira Yesu.
Palibe chimene tingaphunzireko kwa akatswiri azamalamulo. Tiyenera kuphunzira za chikhulupiliro cha uzimu. Tifunikira kuganizira chifukwa chake Yesu anayenera kubatizidwa ndi kukhetsa mwazi pa Mtanda, ndi kufuna chilengedwe cha uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Tiyenera kuyesa kupeza mayankho a mafunso amenewo choyamba, ndiyeno tiyese kufalitsa uthenga wabwino ku anthu onse a kudziko lapansi, kotero kuti mwina angabadwe mwatsopano. Tiyenera kupereka miyoyo yathu ku ntchito yauzimu.
Ngati olalika akuuzani kuti, “Khalani monga munthu wachichepere Chudal Bay. Sungani tsiku lasabata likhale Lopatulika,” akungofuna kuyesa kuti mwina mungapite ku mpingo patsiku lasabata.
Pano palinso nkhani ina imene ingatsimikize kuti zimveke bwino. Panali mkazi wina amene ankayenda m’mayesero ambiri pakupita ku mpingo tsiku lamulungu. Makolo ake ompeza sanali Akristu, ndipo anayesa kwambiri kumuletsa iye kuti asapite ku mpingo. Anali kumuuza kuti azigwira ntchito lamulungu. Koma ankapita m’minda loweruka usiku ndi kugwira ntchito motsogozedwa ndi kuwala kwa mwezi kotero kuti abanja asakhale ndi chomunenera kuti amuletse kusapita ku mpingo lamulungu.
Indedi, ndikofunikira kupita ku mpingo, koma Kodi ndi kokwanira kupita kukapembeza lamulungu lililonse pongofuna kuonetsa m’mene kukhulupilika kwathu kulili? Achikhulupiliro choona ndi obadwa mwa madzi ndi Mzimu. Chikhulupiliro choona chimayamba pamene munthu wabadwa mwatsopano.
Kodi mungapulumutsidwe ku machimo anu mwa kukhala mwa lamulo la Mulungu? Ai. Sindikukuuzani kuti munyalanyaze lamulo, Koma tonse tikudziwa kuti paumunthu ndizosatheka kusunga ndime zonse za lamulo.
Yakobo 2:10 akunena kuti, “Pakuti amene ali yense angasunge malamulo onse, koma akakhumudwa pa limodzi iyeyu wacimwira onse.” Motero yambani mwaganiza m’mene mungabadwire mwatsopano mwa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Ndiyeno, pitani ku mpingo kumene mungamvere uthenga wabwino. Mungakhale ndi umoyo wachikhulupiliro pambuyo pakuti mwabadwa mwatsopano. Ndiyeno, pamene Ambuye waitana, mungapite pamaso pake mwachimwemwe.
Musataye nthawi yanu kupita ku mpingo wabodza, musataye ndalama yanu kupanga nsembe zosocheretsa. Ansembe abodza sangakuletseni inu kupita ku gehena. Choyamba mverani uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndi kubadwa mwatsopano.
Ganizirani chifukwa chimene Yesu anabwerera pa dziko lapansili. Ngati tingalowe mu ufumu wa Kumwamba mwa kukhala mogwirizana ndi lamulo, sakanabwera kudziko lapansili. Pamene anabwera, unsembe unasintha. lamulo linakhala chinthu chakale. Tisanapulumutsidwe, tinkaganiza kuti tingapulumutsidwe mwa kukhala mogwirizana ndi lamulo. Koma ichi sichilinso chizindikiro cha chikhulupiliro choona.
Yesu anatipulumutsa ku machimo onse a dziko ndi chikondi Chake, ndi madzi a ubatizo Wake, ndi mwazi komanso Mzimu Wake. Iye anakwaniritsa chipulumutso chathu kudzera mu ubatizo Wake pa Yordano, mwazi wake wa pa Mtanda, ndiponso kuukanso Kwake.
Mulungu anaika pambali malamulo akale chifukwa anali ofoka ndiponso opanda ntchito. “Pakuti cilamulo sicinacitira kanthu kakhale kopanda cirema, ndipo kulinso kulowa naco ciyembekezo coposa, cimene tiyandikira naco kwa Mulungu. Ndipo monga momwe sikudacitika kopanda lumbiro” (Ahebri 7:19-20). Yesu anapanga lumbiro ndi kupulumutsa ife ku machimo athu onse ndi ubatizo Wake komanso mwazi. Kufera chikhulupiliro kupyolera mu chilamulo ndi imfa yopanda ntchito, ndipo chikhulupiliro choona chokha ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Tiyenera kukhala ndi chikhulupiliro chobala zipatso. Kodi muganiza kuti ndi chiyani chabwino cha moyo wanu? Kodi kungakhale kwabwino kupezeka pa mpingo nthawi zonse ndi kukhala mwa lamulo, kapena kungakhale kwabwino kupezeka ku mpingo wa Mulungu kumene uthenga wabwino wakubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu ukulalikidwa, kotero kuti mubadwenso mwatsopano? Kodi ndi mpingo uti ndiponso ndi olalika otani amene angapindulitse kwambiri moyo wanu? Ganizani zimenezi ndipo sankhani imene muona kuti ndi chabwino ku moyo wanu.
Mulungu anapulumutsa moyo wanu kudzera mu olalika amene ali ndi mawu a uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Aliyense ayenera kuyang’anira moyo wake. Okhulupilira wanzeru oona ndi iye amene amaika moyo wake ku mawu a Mulungu.
YESU ANAKHALA WANSEMBE KUDZERA MU LUMBIRO
Kodi mbumba ya ndondomeko ya Levi inakhala ansembe kudzera mu lumbiro?
Ai. Yesu yekha ndi amene anakhala wansembe kudzera mu lumbiro.
Ahebri 7:20-21 anena kuti, “Ndipo monga momwe sikudacitika kopanda lumbiro; (pakuti iwotu anayesedwa ansembe kopanda lumbiro; koma Iye ndi lumbiro mwa Iye amene ananena kwa Iye, walumbira Ambuye ndipo sadzalapa, Iwe ndiwe wansembe nthawi yosatha.)”
Ndiponso Masalimo 110:4 anena kuti, “Yehova walamulira, ndipo sadzasintha, Inu ndinu wansembe kosatha monga mwa cilongosoko ca Melikizedeke.” Mulungu anapanga lonjezo. Iye anapanga pangano ndi ife kudzera m’mawu olembedwa. “Ndizakhala Wamkulu Wansembe osatha mu ndondomeko ya Melikizedeki. Melikizedeki ndi mfumu yachilungamo, mfumu ya mtendere ndiponso wamkulu wansembe wamuyaya. Ine ndizakhala Wamkulu Wansembe osatha mu ndondomeko ya Melikizedeki pa chipulumutso chanu.”
Yesu anabwera kudzikoli ndipo anakhala Nkhoswe ya pangano labwino. (Ahebri 7:22). M’malo mwa mwazi wa ng’ombe kapena mbuzi, Iye anadzipereka yekha ngati nsembe mwa kubatizidwa ndi kukhetsa mwazi pa Mtanda kuti atsuke machimo athu onse.
M’nthawi ya Chipangano Chakale, pamene wamkulu wansembe wamwalira, mwana wake ankapitiliza unsembe pamene wakwanitsa zaka makumi atatu. Pamene iye wakalamba ndipo mwana wake wakwanitsa zaka makumi atatu, ankapereka unsembe wake kwa mwana wake.
Panali mbeu zambiri za akulu ansembe. Choncho Davide anaika ndondomeko imene onse anayenera kutsatira motsatana. Monga mbeu zonse za Aroni zinasankhidwa kukhala ansembe, anali ndi ufulu ogwira ntchito yakutumikira unsembe. Luka anati, “Zakariya, wa gulu la nsembe la Abiya…ndipo panali, pakucita iye nchito yakupereka nsembe m’dongosolo la gulu lace, pamaso pa Mulungu…”
Yesu anabwera kudzikoli ndi kutenga utumiki wa unsembe kwamuyaya. Iye anabwera ngati Wansembe wa zinthu zabwino ziri nkudza. Iye anakwaniritsa chipulumutso cha kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.
Mbeu za Aroni zinali zofoka ndiponso zoperewera ku thupi lawo. Kodi chinkachitika ndi chiyani wamkulu wansembe akamwalira? Mwana wake anali kutenga unsembe wake, koma nsembe zotere sizinali zokwanira kuti zitsimikize chipulumutso cha mtundu wa anthu. Chikhulupiliro kudzera mu mtundu wa anthu sichingakhale choona komanso kukhala chikhulupiliro chanthunthu.
M’nthawi ya Chipangano Chatsopano, Yesu anabwera kudzikoli. Koma sakanafunikira kupereka nsembe mopitilira chifukwa amakhala kwamuyaya. Iye anachotsa machimo athu kwamuyaya ndi ubatizo Wake. Iye anadzipereka yekha ndipo anapachikidwa kupanga onse amene akhulupilira mwa Iye kukhala omasuka ku uchimo kotheratu.
Tsopano, Iye ndi wamoyo ndipo wakhala kudzanja lamanja la Mulungu akunenera kwa ife. “Atate okondedwa, angakhalebe operewera, koma akukhulupilira mwa Ine. Kodi sindinachotse machimo awo kale kalelo?” Yesu ndi Wamkulu Wansembe wosatha wa chipulumutso chathu.
Ansembe a padziko lapansi sanali anthunthu. Pamene amwalira, ana awo ankatenga unsembe wawo. Ambuye wathu akukhala kwamuyaya. Iye anakwaniritsa chipulumutso chathu chosatha mwa kubwera ku dzikoli, kubatizidwa ndi Yohane Mbatizi, ndiyeno anakhetsa mwazi pa Mtanda chifukwa cha machimo athu.
“Koma pomwe pali cikhululukiro ca macimo palibenso copereka ca kwa ucimo” (Aheberi 10:18). Yesu anachitira umboni ku chipulumutso chathu kufikira kutha kwa nthawi. Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu?
“Pakuti mkulu wa ansembe wotere anatiyenera ife, woyera mtima, wopanda coipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa, wakukhala wopitirira miyamba” (Ahebri 7:26).“Pakuti cilamulo cimaika akuru a ansembe anthu, okhala naco cifoko; koma mau a lumbirolo amene anafika citapita cilamulo, anaika Mwana, woyesedwa wopanda cirema ku nthawi zonse.” (Aheberi 7:28).
Chimene ndikufuna kukuuzani ndi chakuti Yesu Kristu, opanda choipa, anatsuka machimo athu kamodzi kokha kudzera mu madzi a ubatizo Wake ndiponso mwazi Wake pa Mtanda. Iye anatipulumutsa ku machimo athu onse osati chifukwa cha ntchito za lamulo, koma mwa kuchotsa machimo athu onse ndi kuweruzidwa kwamuyaya.
Kodi mukhulupilira kuti anatipulumutsa ku machimo athu onse kudzera mu chipulumutso chosatha? Ngati mumatero, ndinu opulumutsidwa. Koma ngati simutero, mudakali ndi zambiri zoti muphunzire pa chipulumutso chosatha cha Yesu.
Chikhulupiliro choona chikuchokera ku uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, chokhazikika mu Malemba. Yesu Kristu, Mkulu wa ansembe wamuyaya wa kumwamba, anakhala Mpulumutsi wathu osatha kudzera mu ubatizo Wake ndiponso mwazi Wake pa Mtanda.
TIYENERA KUMVETSETSA MWATHUNTHU CHIKHULUPILIRO CHATHU
Kodi chikutanthauza chiyani “kukhulupilira mwa Yesu?”
Kukhala ndi chikhulupiliro mu ubatizo wa Yesu ndi imfa Yake ya pa Mtanda.
Tiyenera kuganiza m’mene tingakhulupilire mwa Yesu m’njira yoyenera ndi kuika chikhulupiliro chathu molondola. Kodi tingakhulupilire bwanji mwa Yesu m’njira yabwino komanso yoyenera? Tingatero mwa kukhulupilira mu uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda.
Chikhulupiliro choyenera ndi kukhulupilira mu ntchito ya Yesu, ubatizo Wake ndi mwazi, popanda kuikako maganizo athu olakwika. Kodi mumakhulupilira zimenechi kukhala zoona? Kodi khalidwe lanu lauzimu lili bwanji? Kodi mumadalira kwambiri pa ntchito ndi mphamvu zanu?
Sinthawi yaitali imene yapita pamene ndinayamba kukhulupilira mwa Yesu, koma ndinavutika kwa zaka khumi chifukwa cha lamulo. Motero ndinatopa ndi moyo otero. Sindifuna ngakhale n’komwe nkukumbukira za nthawi imeneyo. Mkazi wanga wakhala pano tsopano. Akudziwa m’mene zinalili zovuta kwa ife.
Lamulungu lililonse, ndinkanena kuti, “Wachikondi, tiye tikondwere tsiku la lero.”
“Koma lero ndi lamulungu!”
Sankachapa nkomwe zovala lamulungu. Lamulungu, zovala zanga zamkati zinali zakuda. Koma ankandiuza kuti ndiyembekeze kufikira Lolemba. Mwa choona, ndinali oyamika kuti tikusunga Sabata moyenerera. Koma zinali zolimba. Sitinkapuma lamulungu chifukwa kunali kovuta kusunga Sabata moyenerera. Ndikukumbukirabe masiku amenewo.
Okondedwa abwenzi, kuti tikhulupiliredi mwa Yesu, tiyenera kukhulupilira mu chotetezera cha machimo kudzera mu ubatizo ndi mwazi Wake pa Mtanda. Chikhulupiliro choona ndi kukhulupilira mu umulungu ndi umunthu wa Yesu ndi zinthu zonse anachita m’dzikoli.
Kodi zikutanthauzanji “kukhulupilira mwa Yesu?” Ndi kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Pali chinthu choonekeratu apa. Chimene tiyenera kuchita ndi kuyang’ana mu Baibulo ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino. Tonse tiyenera kukhulupilira mu njira yoyenera.
“Zikomo, Ambuye. Tsopano ndaona kuti sizichitika kudzera mu mphamvu zanga! Pakuti uchimo udziwika ndi lamulo (Aroma 3:20). Tsopano ndazindikira zimenezi. Ndinkaganiza kuti chifukwa chakuti lamulo linali labwino, chifukwa linali lamulo la Mulungu, ndiyenera kuyesa kukhala mwa lamuloli. Ndinayesa kwambiri kufikira tsopano, koma ndaona tsopano kuti ndinali kulakwitsa kuganiza kuti ndiyenera kukhala mwa Lamulo. Ndaona tsopano kuti sindingathe kusunga malamulo a Mulungu! Motero, kudzera mu Lamulo la Mulungu, tsopano ndazindikira kuti mtima wanga ndi wodzala ndi maganizo oipa ndi zolakwa. Tsopano ndazindikira kuti Lamulo linaikidwa mwa ife kuti lidziwitse nzeru yauchimo. Oho, zikomo, Ambuye. Sitinazindikire bwino chifuniro Chanu ndipo ndayesa molimba kusunga Lamulo. Unali mwano chabe ngakhale kuyesa kokha. Ndikulapa. Tsopano ndaziwa kuti Yesu anabatizidwa ndi kukhetsa mwazi chifukwa cha chipulumutso changa! Ndakhulupilira!”
Muyenera kukhulupilira moyenera ndiponso moona. Muyenera kukhulupilira mu mawu okha olembedwa mu Baibulo. Ndi njira yokhayo imene mungabadwire mwatsopano kwanthunthu.
Kodi kukhulupilira mwa Yesu nkotani? Kodi ndi chinthu chimene tiyenera kumaliza pa nthawi yoikika? Kodi chikhulupiliro chathu ndi chipembezo chimene tiyenera kugwirirapo ntchito iliyonse? Anthu apanga milungu, ndipo apanganso zipembezo zimene zikuyenerana ndi milungu imeneyo. Chipembezo ndi ndondomeko imene anthu amagwirira ntchito kuti apeze cholinga chawo; kuti akondweretse zabwino za munthu.
Ndiyeno kodi chikhulupiliro n’chiyani? zikutanthauza kukhulupilira mwa Mulungu ndi kuyang’ana kwa Iye. Tikuyang’ana ku chipulumutso cha Yesu ndi kumuyamika Iye chifukwa cha dalitso limeneli. Ichi ndiye chikhulupiliro choona. Izi ndi zosiyana pakati pa chikhulupiliro ndi chipembezo. Pamene mutha kusiyanitsa pakati pa ziwirizi, mudzapeza kumvetsetsa kwakukuru chifukwa cha kuzindikira kwanu kwa chikhulupiliro
Adzipembezo amene sanabadwe mwatsopano amatiuza kuti tiyenera kukhulupilira mwa Yesu ndi kukhala mwa chipembezo. Kodi munthu angakhale okhulupirika mwa kukhala kokha m’chipembedzo? Indedi tiyenera kukhala abwino. Kodi ndani Amene akukhala kwambiri mokhulupilika kuposa ena a ife amene tinabadwa mwatsopano?
Koma mfundo ndi yakuti akunena zimenezi kwa ochimwa. Kuli mitundu khumi ndi iwiri ya machimo pa onse ochimwa. Kodi angakhale bwanji okhulupilika? Zoona, maganizo ake atha kudziwa chimene akufunika kuchita, koma mtima wake sunganyamule chimenecho. Pamene ochimwa watuluka mkachisi, kukhala, mwachipembedzo imakhala nkhani chabe, ndipo chikhumbo chake chimamupereka ku uchimo.
Motero tiyenera kuganiza mu mitima yathu ngati tingakhale mwa lamulo kapena kupulumutsidwa mwa kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda, mwa kukhala ndi chikhulupiliro mu Mkulu Wansembe wamuyaya wa Ufumu wa Kumwamba.
Kumbukirani kuti Yesu ndi Mkulu Wansembe weniweni wa iwo amene akukhulupilira. Tiyeni tonse tipulumutsidwe mwakudziwa ndi kukhulupilira mu chipulumutso choona kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda.
WOBADWA MWATSOPANO SAKUCHITA MANTHA NDI KUTHA KWA DZIKO
Chifukwa chiyani obadwa mwatsopano sakuopa kutha?
kwa dziko Chifukwa chikhulupiliro chawo mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu chawamasula iwo ku uchimo.
Pamene mwabadwadi mwatsopano, simuyenera kuopa kutha kwa dziko pamene likupita kumapeto. Akristu ambiri mu Koriya ankanena kuti dziko lingafike kumapeto pa 28 okotobala, 1992. Ndi tsiku lamsokonezo ndiponso loopsa chotani m’mene lizakhalira, anatero. Koma zonena zawo zinatembenuka kukhala zabodza. Obadwadi mwatsopano akukhala mokhulupilika, kulalikira uthenga wabwino kufikira pomaliza. Nthawi iliyonse pamene dzikoli likutha, chimene tiyenera kuchita ndi kulalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Pamene mkwati afika, akwatibwi amene ndi obadwadi mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu angakumane naye mwachimwemwe chachikulu, ndikunena kuti, “Oho, mwabwera tsopano! Thupi langa likali loperewera, koma munandikonda ndikundipulutsa kumachimo anga onse. Choncho ndilibe uchimo mu mtima mwanga. Zikomo, ambuye. Ndinu Mpulumutsi wanga!”
Yesu ndi mkwati wauzimu wa olungama onse. Ukwati unachitika chifukwa mkwati anakonda mkwatibwi, osati mosemphanitsa. Ndikudziwa kuti nthawi zina zimachitika choncho m’dzikoli, koma Kumwamba, ndi mkwatibwi amene amasankha kuti ukwati uchitike. Ndi mkwati Yesu amene anasankha kuti akwatire kuchoka pa chikondi Chake ndi chipulumutso chake chimene anapereka, zilibe kanthu kuti mkwatibwi ndi otani. Umu ndi m’mene ukwati umapangidwira Kumwamba.
Mkwati akudziwa zonse za mkwatibwi. Chifukwa akwatibwi ake okondedwa anali ochimwa, Iye anamva chisoni ndi iwo ndipo anawapulumutsa ku uchimo onse mwa kubatizidwa ndi kukhetsa mwazi pa Mtanda.
Ambuye wathu Yesu sanabwere padzikoli ngatio mbeu ya Aroni. Iye sanabwere kudzikoli kudzapereka nsembe ya dziko lapansi. Kunali Alevi ambirimbiri, mbeu za Aroni, kuti zigwire ntchito.
Zoona zake, mwini nsembe mu Chipangano Chakale sanali oposa wina koma Yesu mwini wake. Motero, pamene chinthu cheni cheni chinabwera kudzikoli, kodi n’chiyani chinachitika ku chithunzithunzi chake? Chithunzithunzi chinaikidwa pambali.
Pamene Yesu anabwera kudzikoli, sanapereke nsembe monga anachitira Aroni. Anadzipereka Yekha chifukwa cha mtundu wa anthu mwa kubatizidwa ndi kukhetsa mwazi chifukwa cha chipulumutso cha ochimwa. Iye anakwaniritsa chipulumutso pa Mtanda.
Kwa iwo amene akukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda, chipulumutso chidzabwera mopanda ziyenerezo zina zilizonse. Yesu sanatetezere machimo athu mwa njira yosaoneka bwino. Iye anachita izi poyera. “Ine ndine njira, coonadi, ndi moyo” (Yohane 14:6). Yesu anabwera kudzikoli ndi kupulumutsa ife ndi ubatizo Wake, imfa Yake, ndiponso kuuka Kwake.
CHIPANGANO CHAKALE NDI CHITSANZO CHA YESU
Kodi ndi chifukwa chiyani kukhazikitsa pangano lina?
Chifukwa pangano loyamba linali lodwala komanso lopanda ntchito.
Chipangano Chakale ndi chithunzithunzi cha Chipangano Chatsopano. Ngakhale kuti Yesu sanapereke nsembe monga akulu a ansembe a m’Chipangano Chakale, iye anatumikira unsembe wabwino, unsembe wakumwamba osatha. Chifukwa anthu m’dzikoli ali ochimwa kuyambira pakubadwa kwawo, akhala ochimwa, ndipo sangakhale olungama kudzera mu lamulo la Mulungu. Motero Mulungu anakhazikitsa pangano lina.
Atate wathu Wakumwamba anatuma Mwana Wawo obadwa Yekha ku dzikoli ndi kutiuza ife mobwezera kuti tikhale ndi chikhulupiliro mu ubatizo Wake, mwazi Ake, ndiponso kuukanso Kwake. Ili ndi pangano lachiwiri la Mulungu. Pangano lachiwiri likufuna ife kuti tikhulupilire mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Ambuye sakufunsanso ntchito zathu yabwino. Samatiuza m’mene tifunikira kukhalira kuti tipulumutsidwe. Iye amatiuza kokha kuti tikhulupilire mu chipulumutso kudzera mwa Mwana Wake. Iye amatiuza kuti tikhulupilire mu ubatizo Wake komanso mwazi Wake pa Mtanda pa zonse. Ndipo tiyenera kunena kuti inde.
Mu Baibulo, nyumba ya Yuda inasunga ufumu. Mafumu onse a Israyeli anabadwira m’nyumba ya Yuda kufikira Mfumu Solomo. Ngakhale pambuyo pa kugawikana kwa ufumu, nyumba ya Yuda inagwira ufumu wakumwera kufikira kugwa kwake mu 586 B.C. Mwa njira imeneyi, anthu a Yuda anaimilira Aisrayeli. Mtundu wa Levi unali m’modzi wa ansembe. Mtundu ulionse wa Israyeli unali ndi ndondomeko yake. Mulungu analonjeza mtundu wa Yuda kuti Yesu azauka ku mphamvu Zake.
Kodi ndi chifukwa chiyani anapanga pangano limeneli ndi mtundu wa Yuda? Kupanga pangano limeneli kunali chimodzi modzi ndi kupanga pangano ndi anthu onse a dziko lapansi chifukwa Israyeli akuimira anthu onse m’dziko lapansi. Yesu anakwaniritsa pangano latsopano, limene linali chipulumutso cha mtundu wa anthu kudzera mu ubatizo Wake, imfa Yake ya pa Mtanda, ndiponso kuuka Kwake.
MACHIMO A ANTHU SANGATSUKIDWE NDI KULAPA
Kodi machimo a munthu amatsukidwa ndi kulapa?
Ai.
Mu Yeremiya 17:1, kunalembedwa kuti uchimo wa munthu aliyense umalembedwa m’malo awiri. “Cimo la Yuda lalembedwa ndi peni lacitsulo, ndi nsonga ya diamond; lalembedwa pa colembapo ca m’mtima mwao, ndi pa nyanga za maguwa ansembe anu..”
Machimo athu analembedwa m’mitima yathu. Umo ndi m’mene tikudziwira kuti ndife ochimwa. Pamene wina asanayambe kukhulupilira mwa Yesu, sadziwa kuti iye ndi ochimwa. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti lamulo la Mulungu mulibe mu mtima wake. Motero, pamene munthu ayamba kukhulupilira mwa Yesu, amazindikira kuti ndi ochimwa pamaso pa Mulungu.
Ena amazindikira kokha kuti ndi ochimwa zaka khumi pambuyo pakuti akhulupilira mwa Yesu. “Oho, okondedwa! Ine ndine ochimwa! Ndinaganiza kuti ndinapulumutsidwa, koma mwinamwake ndinebe ochimwa.” Kuzindikira kumabwera tsiku limodzi lokha pamene tadzizindikiradi tokha m’mene tilili. Anakhala okondwa zaka khumi zokha, koma mwadzidzidzi anaona choonadi. Kodi mudziwa chifukwa? Kuzindikira kumeneku kunabwera chifukwa machimo awo oona ndi zolakwa zao pomaliza zinapangidwa poyera kudzera mwa lamulo la Mulungu. Munthu otere anakhulupilira mwa Yesu kwa zaka khumi kopanda kubadwanso mwatsopano.
Ochimwa otere sangafufute machimo ake mu mtima wake, akhalabe ochimwa pamaso pa Mulungu. Ena amatha zaka zisanu, ndipo ena amatha zaka khumi kuti afike pakuzindikiraku. Ena amazindikira zitatha zaka makumi atatu, ena makumi asanu, ndipo ena samazindikira nkomwe choonadi kufikira chimaliziro. “Okondedwa Mulungu, ndinali kukhala wabwino ndisanakhale ndi malamulo mu maganizo anga. Ndinali ndi chilimbikitso kuti ndikusunga Chilamulo Chanu bwino, koma tsopano ndazindikira kuti ndimacimwa masiku onse. Monga m’mene ananenera Mtumwi Paulo ‘Ndipo kale ine ndinali wamoyo popanda lamulo; koma pamene lamulo linadza, ucimo unatsitsimuka, ndipo ine ndinafa’ (Aroma 7:9). Ndine ochimwa ngakhale kuti ndikukhulupilira mwa Yesu.”
Ndi machimo anu amene akuletsani inu kukhala mwa mawu a Mulungu. Machimo anu analembedwa mu mtima wanu. Chifukwa chakuti Mulungu analemba machimo anu kumeneko, pamene mukuweramitsa mutu wanu kuti mupemphere, machimo anu onse amachoka. “Chodabwitsa! Ine ndi uchimo umene munachita.”
“Koma ndinakutetezerani inu zaka ziwiri zapitazo. Kodi chifukwa chiyani mukuzionetsera nokha modzidzimutsa? Kodi chifukwa chiyani simunachoke?”
“Oho, musakhale oipa! ndinalembedwa mu mtima wanu. Zilibe kanthu kuti mukuganiza chiyani, mukali ochimwa.”
“Ai! Ai!”
Choncho, ochimwa amalapanso chifukwa cha machimo anachita zaka ziwiri zapitazo. ‘Chonde ndikhululukireni, Ambuye. Ndidakali ndili kusautsidwa ndi machimo ndinachita kale. Ndinalapa machimo anga, koma akali ndi ine. Chonde ndikhululukireni ine, popeza ndachimwa.”
Koma kodi machimowo amachoka ndi kulapa? Chifukwa machimo a anthu analembedwa mu mitima yawo, sangafufutidwe popanda uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Pokhapo kudzera mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndi pamene chitetezero cha machimo choona chingaoneke. Tingapulumutsidwe kokha kudzera mu chikhulupiliro chathu mu uthenga wabwino weniweni wa Yesu.
NDIZAKHALA MPULUMUTSI WANU
Kodi tiyenera kuyankha bwanji Pa za pangano latsopano
Tiyenera kukhulupilira mwa ilo mu mitima yathu ndi kulilalikira padziko lonse lapansi.
Ambuye wathu wa Kumwamba anapanga pangano latsopano ndi ife. “Ndizakhala Mpulumutsi wanu. Ndizakupanganu kumasuka kotheratu ku machimo onse a dziko kudzera mwa madzi ndi mwazi. Ndidzadalitsadi moona onse amene akukhulupilira mwa Ine.”
Kodi mumakhulupilira mu pangano latsopano pamodzi ndi Mulungu? Tingapulumutsidwe ku machimo athu onse ndi kukhala obadwa mwatsopano pamene takhulupilira mu choonadi cha pangano Lake ndiponso chipulumutso Chake kudzera mwa madzi ndi mwazi.
Sitimakhulupilira dotolo ngati sadziwa vuto lathu bwino. Dotolo choyamba ayenera kudziwa molondola vuto la wodwala wake moyenera ndipo aone mankhwala oyenera kumpatsa. Pali mankhwala ambirimbiri, koma dotolo ayenera kudziwa bwino amene ayenera kugwiritsa ntchito. Pamene dotolo wathandiza odwala wake moyenera, pali mankhwala ambiri amene angawachiritse. Koma kusadziwa bwino matenda kungapangitse mankhwala abwino kupanganga wodwalayo kudwala kwambiri.
Chimodzimodzi, pamene mukukhulupilira mwa Yesu, muyenera kudziwa vuto la mzimu wanu ulili kulingana ndi mawu a Mulungu. Pamene mukuyeza mzimu wanu ndi mawu a Mulungu, mungaone bwino bwino m’mene mzimu wanu ulili. Dotolo wauzimu angachilitse odwala ake kopanda kusankha. Onse angabadwe mwatsopano.
Ngati munganene, “Sindikudziwa kuti mwina ndinaomboledwa,” zikutanthauza kuti simunapulumutsidwe. Ngati m’busa ndi mtumwi wa Yesu weniweni, ayenera kukwanitsa kuthana ndi mavuto ya uchimo wa otsatira ake. Ndiyeno, angapitilize kuthana ndi mavuto a chikhulupiliro chawo ndi kuwatsogolera iwo mwauzimu. Ayenera kutha kuona bwino khalidwe la uzimu wa otsatira ake.
Yesu anabwera padzikoli kuzachotsa uchimo onse wa dziko. Anabwera ndipo anabatizidwa ndi kufa pa Mtanda. Pamene anatetezera uchimo onse, kodi anasiyako machimo anu? Mawu a madzi ndi Mzimu anachotsa machimo a okhulupilira onse.
Uthenga wabwino uli ngati bomba. Umaphulitsa chilichonse kuyambira nyumba yaitali kufikira ku mapiri. Ntchito ya Yesu ili ngati chimenechi. Iye amasesa machimo a iwo amene akhulupilira mwa Iye ndi uthenga Wake Wabwino wa madzi ndi Mzimu. Tiyeni tsopano tione pa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu monga ananenera Mbaibulo.
UTHENGA WABWINO WA KUIKA MANJA MU CHIPANGANO CHAKALE
Kodi cholinga choika manja mu Chipangano Chakale chinali chiyani?
Cholinga chake chinali kupereka machimo pa nsembe yauchimo
Tiyeni tione pa choonadi cha uthenga wabwino wa kuombola mu Levitiko 1:3-4. “Copereka cace cikakhala nsembe yopsereza ya ng’ombe, azibwera nayo yaimuna yopanda cirema; abwere nayo ku khomo la cihema cokomanako, kuti alandirike pamaso pa Yehova. Ndipo aike dzanja lace pamutu pa nsembe yopsereza; ndipo adzalandiridwa m’malo mwace, imtetezere.
Ndimeyi ikutiuza kuti nsembe yopsereza iyenera kuperekedwa pa khomo la chihema chokomanako pamaso pa Ambuye mwa kuika manja pa mutu pa nsembeyo, ndipo nsembeyo iyenera kukhala nyama yamoyo yopanda chilema.
Mu nthawi ya Chipangano Chakale, ochimwa ankaika manja ake pa nsembe kuti apange chotetezera cha machimo ake a masiku onse. Ankapha nsembe yauchimo pamaso pa Ambuye ndipo wansembe ankatenga mwazi wina ndi kuika pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza. Ndiyeno ankathira mwazi otsala pansi pa guwa ndipo ochimwa ankakhululukidwa uchimo wake wa pa tsiku.
Uchimo wa pa chaka, unalembedwa mu Levitiko 16:6-10, ““Ndipo Aroni abwere nayo ng’ombe ya nsembe ya ucimo, ndiyo yace yace, nacite codzitetezera iye yekha, ndi mbumba yace. Ndipo atenge mbuzi ziwirizo naziimike pamaso pa Yehova pa khomo pa cihema cokomanako. Ndipo Aroni ayese maere pa mbuzi ziwirizo; maere amodzi kwa Yehova, ndi amodzi kwa Azazeli ndipo Aroni abwere nayo mbuzi imene adaigwera maere a Yehova, naiyese nsembe ya ucimo. Koma mbuzi imene adaigwera maere a Azazeli, aiike yamoyo pamaso pa Yehova, kuti acite nayo cotetezera, kuitumiza kucipululu ikhale ya Azazeli.” Monga afotokozera kale mu Baibulo, mbuzi yamoyo ikutanthauza “Kuchotsa.” Choncho uchimo wa pachaka unali kuonongedwa pa tsiku la khumi la mwezi wa chisanu ndi chiwiri.
Mu Levitiko 16:29-30, munalembedwa kuti, “Ndipo lizikhala kwa inu lemba losatha; mwezi wacisanu ndi ciwiri, tsiku lakhumi la mweziwo, muzidzicepetsa, osagwira nchito konse, kapena wa m’dziko, kapena mlendo wakukhala pakati panu; popeza tsikuli adzacitira inu cotetezera, kukuyeretsani; adzakuyeretsani, kukucotserani zoipa zanu zonse pamaso pa Yehova.”
Ili linali tsiku limene Israyeli ankatetezera uchimo wa pachaka. Kodi izi zinali kuchitika motani? Choyamba, mkulu wansembe Aroni ankafunika kukhalapo popereka nsembe. Kodi ndani ankaimira anthu a mu Israyeli? Aroni. Mulungu anasankha Aroni ndi mbumba yake ngati akulu ansembe.
Aroni ankapereka ng’ombe yamphongo kuti adzitetezere yekha ndi mbumba yake. Ankapha ng’ombe ndi kuwaza mwazi wina kuno ndi uko pansi komanso patsogolo pa mpando wachifundo nthawi zisanu ndi ziwiri. Choyamba ankafunika kudzitetezera yekha komanso mbumba yake onse.
Chitetezero cha machimo chikutanthauza kupereka uchimo wa wina ku nsembe yauchimo ndi kuleka nsembe yauchimo kuti ife pa m’malo mwake. Ochimwa ndiye ayenera kufa, koma angatetezere machimo ake mwa kupatsira pa nsembe ndi kuilola kufa m’malo mwake.
Machimo ake komanso ambumba yake akachotsedwa, anali kupereka mbuzi imodzi pamaso pa Mulungu pamene anali kupereka mbuzi ina kuchipululu ngati mbuzi yamoyo pamaso pa anthu a Israyeli.
Mbuzi imodzi inali kuperekedwa ngati nsembe yauchimo. Aroni ankaika manja pamutu pa nsembe yauchimo ndi kuvomereza, “O, Mulungu, Anthu anu a Israyeli anaononga malamulo khumi anu ndi ndime 613 za mu lamulo lanu. Israyeli akhala ochimwa. Tsopano ndikuika manja anga pa mbuziyi kuti ndipereke machimo athu onse a pa chaka.”
Ankadula khosi la mbuzi ndi kulowa mu malo Oyeretsetsa mkati mwa chihema ndi mwazi wake. Ndiyeno anali kuwaza mwazi kuno ndi uko kutsogolo kwa mpando wachifundo kasanu ndi kawiri.
Mkati mwa malo Oyeretsetsa munali likasa la pangano. Chovundikirapo chake cimatchedwa kuti mpando wachifundo, ndipo mkati mwake muli miyala iwiri ya pangano, poto wa golide wa mana, ndi ndodo ya Aroni imene inaphukira.
Ndodo ya Aroni ikuimira kuuka kwa Yesu, miyala iwiri ya chipangano ikuimira chilungamo Chake, ndipo poto wa golide wa mana akutanthauza mawu Ake a moyo.
Pali chovindikira pa likasa la chipangano. Mwazi ankathiridwa pa mpando wachifundo kasanu ndi kawiri. Popeza panali ma belu a golide omwe ankamangiliridwa pa nsonga ya mkanjo wa mkulu wansembe ndipo ankalira pomwe mwazi anali kuwazidwa.
Mu Levitiko 16:14-15, kunalembedwa kuti, “Ndipo atengeko mwazi wa ng’ombeyo, ndi kuuwaza ndi cala cace pacotetezerapo, mbali ya kum’mawa; nawaze mwazi ndi cala cace cakuno ca cotetezerapo kasanu ndi kawiri. Pamenepo aiphe mbuzi ya nsembe yaucimo, ndiyo yophera anthu, nalowe nao mwazi wace m’tseri mwa nsaru yocinga, nacite nao mwazi wace monga umo anacitira ndi mwazi wa ng’ombe, nawauze pacotetezerapo ndi cakuno ca cotetezerapo.”
Mabelu anali kulira nthawi zonse pamene anali kuwaza mwazi wa mbuzi, ndipo Israyeli onse amene anali kusonkhana kubwalo anali kumva kulilako. Popeza chitetezero cha machimo awo chinkayenera kuchitika kudzera mwa mkulu wansembe, kulira kwa mabelu kunkatanthuza kuti machimo awo akhululukidwa. Kunali kulira kwa dalitso la anthu onse a mu Israyeli.
Pamene mabelu analira kasanu ndi kawiri, iwo ankanena kuti, “Tsopano ndatsitsimutsidwa. Ndinali ndi nkhawa chifukwa cha uchimo wa chaka chonse, koma tsopano ndakhala omasuka.” Ndipo anthu ankabwerera ku m’makhalidwe awo, akuzimva omasuka ku mlandu. Kulira kwa mabelu nthawi imeneyo kunali ngati uthenga wabwino wa kubadwanso mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.
Pamene tamvera uthenga wabwino wa chiombolo cha madzi ndi Mzimu ndi kukukhulupirira ndi mitima yathu yonse ndi kuuvomereza ndi pakamwa pathu, izi ndi zimene uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ulili. Pamene belu lalira kasanu ndi kawiri, machimo onse a pa chaka a Israyeli anali kuyeretsedwa. Machimo awo ankatsukidwa pamaso pa Mulungu.
Akapereka nsembe ya Israyeli, mkulu wansembe ankatenga mbuzi ina ndi kupita ku anthu ake akuyembekezera kubwalo la chihema. Pamene anali kuona, mkulu wansembe Aroni ankaika manja pamutu pa mbuzi inayo.
Mu Levitiko 16:21-22, “Ndipo Aroni aike manja ace onse awiri pamutu pa mbuzi yamoyo, ndi kubvomereza pa iyo mphulupulu zonse za ana a Israyeli, ndi zolakwa zao zonse,monga mwa zocimwa zao zonse; naike izi pamutu pa mbuziyo, ndi kuitumiza kucipululu ndi dzanja la munthu wompangiratu, ndi mbuziyo isenze yokha mphulupulu zonsezo kumka nazo ku dziko la pa lokha; ndipo azitaya mbuziyo m’cipululu.”
Mkulu wansembe, Aroni, ankaika manja ake pamutu pa mbuzi inayo (mbuzi yamoyo) ndi kuulula machimo onse a pa chaka a Israyeli pamaso pa Mulungu. “O Mulungu, Israyeli anachimwira Inu. Tinaononga malamulo khumi ndi ndime 613 za lamulo lanu. O Mulungu, ndikupereka machimo onse a pa chaka a Israyeli pamutu pa mbuziyi.”
Mogwirizana ndi Yeremiya 17:1, machimo amalembedwa m’malo awiri. Imodzi mu Buku la ntchito, ndipo lina pansi pa mitima yawo.
Choncho ngati anthu akutetezera machimo awo, machimo awo ayenera kufufutidwa mu Buku la ntchito ndiponso pansi pa mitima yawo. Pa Tsiku Lachitetezero cha machimo, mbuzi imodzi inali ya machimo olembedwa mu Buku la Chiweruzo ndipo inayo inali ya iwo amene inalembedwa pansi pa mitima yawo.
Kodi Mulungu anaonetsa chiyani Israyeli kudzera mu ndondomeko Yoperekera nsembe mu Chipangano Chakale?
Kuti Mpulumutsi adzabwera ndi kuchotsa machimo awo kamodzi kokha m’njira yabwino kwambiri
Mwa kuika manja pamutu pa mbuzi, mkulu wansembe ankaonetsa anthu kuti machimo awo a pa chaka aperekedwa pa mbuzi. Pamene machimo ankaikidwa pamutu pa mbuzi, munthu wina wompangiratu ankatsogolera mbuzi ku chipululu.
Palestina ndi malo achipululu. Mbuzi imene inkanyamula machimo onse a pa chaka a Israeli inali kutsogoleredwa ndi munthu amene anasankhidwiratu kuti agwire ntchito ya kuchipululu kumene kunalibe madzi kapena msipu. Anthu ankaima ndi kuona mbuzi yamoyo ikupita kuchipululu.
Paokha anali kunena kuti, “Ndikanafa ine, koma mbuzi ndiye yafa m’malo mwa machimo anga. Mphotho ya uchimo ndi imfa, koma mbuzi yafa m’malo mwa ine. Zikomo kwambiri, mbuzi. Imfa yako ikutanthauza kuti ndingathe kukhala ndi moyo.” Mbuzi inkatsogoleredwa kutali m’chipululu ndipo a Israyeli anali kukhululukidwa tchimo lawo la chaka chonse.
Pamene uchimo mu mtima mwanu waperekedwa ku nsembe yauchimo, ndiye kuti mwayeretsedwa. Ndi choncho zosavuta. Choonadi chimakhala chosavuta ngati tamvetsetsa basi.
Mbuzi inkasowa mkati mwa chipululu. Munthuyo ankabwerera yekha akaisiya. Machimo onse chaka chonse a Israyeli ankasowa. Mbuzi inkavutika m’chipululu mopanda madzi nkapena msipu, ndipo pothera pake inkafa ndi machimo chaka chonse a Israyeli.
Mphotho ya uchimo ndi imfa, ndipo chilungamo cha Mulungu chinakwaniritsidwa. Mulungu anapereka nsembe mbuzi kuti Israyeli akhale ndi moyo. Zolakwa zonse za Israyeli za pachaka zinatsukidwa ndi kukhala zoyeretsedwa.
Popeza tchimo la tsiku limodzi ndi tchimo la chaka chonse linali kukhululukidwa motero mu nthawi ya Chipangano Chakale, ndi pangano la Mulungu kuti machimo athu chimodzimodzi akhululukidwe kamodzi kokha. Ndi pangano Lake kuti adzatumiza Mesiya ndi kuombola ife ku machimo a moyo wathu wonse. Pangano linachitika kudzera mu ubatizo wa Yesu.
KUBADWA MWATSOPANO MWA MADZI NDI MZIMU MU CHIPANGANO CHATSOPANO
Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anabatizidwaa ndi Yohane Mbatizi?
Kuti akwaniritse chilungamo chonse mwa kuchotsa machimo onse a dziko. Ubatizo wa Yesu mu Chipangano Chatsopano unali kuika manja mu Chipangano Chakale
Tiyeni tiwerenge Mateyu 3:13-15. “Pamenepo Yesu anacokera ku Galileya nadza ku Yordano kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye. Koma Yohane anati amkanize, nanena, Ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi? Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero. Pamenepo anamlola Iye.”
Yesu anapita ku Yordano ndipo anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi ndipo mwakutero, anakwaniritsa chilungamo chonse. Iye anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Yohane anali wamkulu mwa iwo amene anabada mwa akazi.
Mateyu 11:11-12 anena kuti “Indetu ndinena kwa inu, Sanauke wakubadwa mwa akazi munthu wankuru woposa Yohane Mbatizi. …Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa kumwamba uli wokangamizidwa.”
Yohane Mbatizi anasankhidwa ndi Mulungu kuti akhale oyimilira mtundu wa anthu ndipo anatumizidwa miyezi isanu ndi umodzi Kristu asanabwere. Iye anali mbeu ya Aroni ndiponso mkulu wansembe omaliza.
Yohane Mbatizi anati pamene Yesu anabwera kwa iye, “Ndiyenera kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi?”
“Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero.” Cholinga Chake chinali kumasula mtundu wa anthu ku uchimo kotero kuti athe kukhala ana a Mulungu. Yesu anati kwa Yohane, “Tiyenera kumaliza uthenga wabwino wa kubadwanso mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Choncho ndibatize Ine tsopano.”
Yohane anabatiza Yesu. Kunali koyenera kwa Yesu kubatizidwa kuti achotse machimo onse a dziko. Chifukwa chakuti anabatizidwa m’njira yoyenera kwambiri, tinapulumutsidwa mwangwiro ku machimo athu onse, Yesu anabatizidwa kotero kuti machimo athu onse apatsidwe pa Iye.
Yesu anabwera pa dzikoli ndipo anabatizidwa pamene anali ndi zaka makumi atatu. Unali utumiki Wake oyamba. Yesu anakwaniritsa chilungamo chonse mwa kuchotsa machimo onse a dziko, motero anayeretsa anthu onse.
Yesu anabwera padziko lino ndipo anabatizidwa m’njira yoyenera kwambiri kuti aombole ife ku machimo athu onse. “Motero” chilungamo chonse chinakwaniritsidwa.
Mulungu anati, “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera” (Mateyu 3:17). Yesu anadziwa kuti adzachotsa machimo a mtundu wa anthu ndi kukhetsa mwazi mpaka kufa pa Mtanda, koma Iye analemekeza chifuniro cha Atate Wake, ponena kuti, “Koma si monga ndifuna Ine, koma Inu” (Mateyu 26:39). Cholinga cha Atate chinali chotsuka machimo onse a mtundu wa anthu ndipo mwa ichi anapereka chipulumutso ku anthu a ku dziko.
Choncho Yesu, Mwana omvera, anamvera chifuniro cha Atate Wake ndipo anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi.
Mu Yohane 1:29, “M’mawa mwace anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!”’ Yesu anachotsa uchimo onse ndi kukhetsa mwazi pa Mtanda pa Gologota. “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” Yohane Mbatizi anachitira umboni.
Kodi muli ndi uchimo kapena ai? Kodi ndinu munthu olungama kapena ochimwa? Zoona zake ndi zakuti Yesu anachotsa uchimo wa dziko ndipo anapachikidwa pa Mtanda chifukwa cha ife tonse.
Kodi ndi liti pamene machimo a ochimwa anaperekedwa kwa Yesu?
Yesu ananyamula machimo athu pamene anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi pa Yordano.
Pamene tinabadwa m’dzikoli, timachimwa ngakhale pakati pa chaka chimodzi kufikira khumi. Yesu anachotsa machimo amenewo. Timachimwanso pakati pa zaka khumi ndi chimodzi kufikira makumi awiri. Machimo amene timachita m’mitima yathu ndi m’zochita zathu, Iye anachotsa onse.
Timachimwanso pakati pa zaka 21 ndi 45. Iye anachotsanso amenewo. Iye ananyamula machimo onse a dziko ndipo anapachikidwa pa Mtanda. Timachimwa kuyambira tsiku limene tinabadwa kufikira tsiku lakufa kwathu. Koma Iye anachotsa onse.
“Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” Uchimo onse, kuyambira aja a munthu oyamba, Adamu, kufikira a munthu omaliza amene azabadwe m’dzikoli―kulimonse kumene angapezeke―Iye anachotsa onse. Iye sanaloze ndi kusankha kuti ndi machimo a ndani adzatenge.
Iye sanasankhe kuti akonde ena a ife okha. Iye anabwera mwa thupi ndi kuchotsa machimo onse a dziko ndipo anapachikidwa pa Mtanda. Iye analandira chiweruzo m’malo mwa ife tonse ndi kuchotsa machimo onse a dzikoli kwamuyaya.
Palibe amene anasiidwa ku chipulumutso Chake. “macimo adziko” akuphatikizapo machimo athu onse. Yesu ananyamula onse.
Ndi ubatizo Wake komanso mwazi, anayeretsa machimo onse a dziko. Iye anachotsa kudzera mu ubatizo Wake ndipo anaweruzidwa chifukwa cha machimo athu pa Mtanda. Yesu asanafe pa Mtanda, Iye anati, “Kwatha!” (Yohane 19:30), kutanthauza chipulumutso cha mtundu wa anthu chinatsirizika.
Kodi chifukwa chiyani Yesu anapachikidwa pa Mtanda? Chifukwa chakuti moyo wathupi uli m’mwazi, ndipo mwazi amapanga chitetezero cha moyo wa munthu (Levitiko 17:11). Kodi chifukwa chiyani Yesu anayenera kubatizidwa? Chifukwa chakuti anali kufuna kunyamula machimo onse a dziko lapansi.
“Citapita ici Yesu, podziwa kuti zones zidatha pomwepo kuti lembo likwaniridwe, nanena, Ndimva ludzu .’” (Yohane 19:28). Yesu anafa, podziwa kuti pangano lonse la Mulungu mu Chipangano Chakale linakwaniritsidwa ndi ubatizo Wake pa Yordano ndi imfa Yake pa Mtanda.
Yesu anadziwa kuti chiombolo chinakwaniritsidwa kudzera mwa Iye ndipo anati, “Kwatha!” Iye anafa pa Mtanda. Iye anayeretsa ife, anaukanso kwa akufa pa tsiku lachitatu ndi kukwera Kumwamba, kumene tsopano akukhala kudzanja lamanja la Mulungu.
Kutsukidwa kwa machimo onse kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi imfa Yake ya pa Mtanda ndi uthenga wabwino odalitsika wa kubadwanso kwatsopano kwa madzi ndi Mzimu. Ukhulupilireni, ndipo mudzakhululukidwa ku machimo anu onse.
Sitingatetezere machimo athu mwa kupemphera mapemphero a kulapa masiku onse. Chiombolo chinaperekedwa kamodzi kokha kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi imfa Yake ya pa Mtanda. “Koma pomwe pali cikhululikiro ca macimo palibenso copereka ca kwa ucimo” (Aheberi 10:18).
Tsopano chimene tiyenera kuchita ndi kukhulupilira mu chiombolo kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi kupachikidwa Kwake. Khulupilirani ndipo mudzapulumutsidwa.
Aroma 5:1-2 ananena kuti, “Popeza tsono tayesedwa olungama ndi cikhulupiliro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Kristu; amene ife tikhoza kulowa naye ndi cikhulupiliro m’cisomo ici m’mene tirikuimamo; ndipo tikondwera m’ciyembekezo ca ulemelero wa Mulungu .”
Palibenso njira ina yokhalira olungama koma kukhulupilira mu uthenga wabwino odalitsika wa kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.
CHOLINGA CHA LAMULO LA MULUNGU
Kodi tingayeretsedwe mwa Lamulo?
Ai, sitingatero. Lamulo Lingatipange kokha kukhala odziwa za machimo athu.
Mu Ahebri 10:9, Kunalembedwa kuti, “Pamenepo anati, Taonani, ndafika kudzacita cifuniro canu. Acotsa coyambaco, kuti akaike caciwirico.” Sitingayeretsedwa mwa Lamulo. Likungotipangitsa kukhala ochimwa. Mulungu sanatanthauze kuti tizimvera Lamulo.
Aroma 3:20 anena kuti, “Pakuti ucimo udziwika ndi lamulo” Mulungu anapatsa a Israyeli lamulo kudzera mwa Mose patatha zaka 430 kuyambira pamene Abrahamu analandira Pangano. Iye anawapatsa Lamulo kuti adziwe kuti zikutanthauza chiyani kuchimwa pamaso pa Mulungu. Popanda lamulo la Mulungu, mtundu wa anthu ukanakhala opanda nzeru ya uchimo. Mulungu anatipatsa lamulo Lake kuti tikhale tikuzindikira uchimo.
Choncho cholinga chokha cha lamulo ndi kutipangitsa kuti tidziwe kuti tonse ndife ochimwa pamaso pa Mulungu. Kudzera mu nzeru imeneyi, tinauzidwa kubwerera kwa Yesu mwa kukhulupilira mu dalitso la uthenga wabwino wa kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Ichi ndiye cholinga cha Lamulo la Mulungu limene anatipatsa.
AMBUYE ANABWERA KUZACHITA CHIFUNIRO CHA MULUNGU
Kodi tiyenera kuchita chiyani pamaso pa Mulungu?
Tiyenera kukhulupilira mu chiombolo cha Mulungu kudzera mwa Yesu.
“ndafika kudzacita cifuniro canu. Acotsa coyambaco, kuti akaike caciwirico” (Ahebri 10:9). Chifukwa sitingakhale oyeretsedwa mwa Lamulo, Mulungu sanatiombole ndi Lamulo lake, koma ndi chiombolo Chake chanthunthu. Mulungu anatiombola ndi chikondi Chake komanso chilungamo.
“Ndi cifuniro cimeneco tayeretsedwa mwa copereka ca thupi la Yesu Kristu, kamodzi, kwatha. Ndipotu wansembe ali yense amaima tsiku ndi tsiku, natumikira, napereka nsembe zomwezi kawiri kawiri, zimene sizikhoza konse kucotsa macimo; koma Iye m’mene adapereka nsembe imodzi cifukwa ca macimo, anakhala pa dzanja lamanja la Mulungu cikhalire” (Ahebri 10:10-12).
Iye anakhala kudzanja la manja la Mulungu chifukwa nchito yake ya chiombolo inatha ndipo panalibe china choonjezera chimene Iye anayenera kuchita. Iye sazabatizidwa kapena kuzipereka nsembe Yekha kobwereza kuti apulumutse ife.
Tsopano popeza machimo onse a dziko anatsukidwa, zimene ayenera kuchita ndi kupereka moyo osatha kwa iwo amene akhulupilira mwa Iye. Iye tsopano akuika Mzimu mwa iwo amene akhulupilira mu chipulumutso Chake cha madzi ndi Mzimu.
Yesu anabwera kudzikoli ndi kuchotsa machimo onse ndi kufa pa Mtanda, motero anamaliza ntchito Yake. Tsopano popeza ntchito ya Ambuye inatha, Iye akukhala kuzanja lamanja la Mulungu.
Tiyenera kukhulupilira Ambuye wathu Yesu anapulumutsa ife ku uchimo kwa muyaya. Iye anatipanga kukhala angwiro kwamuyaya ndi ubatizo Wake komanso mwazi.
IWO AMENE AKHALA ADANI A MULUNGU
Kodi adani a Mulungu ndani?
Iwo amene akhulupilira mwa Yesu koma ali ndi uchimo m’mitima yawo.
Mu Ahebri 10:12-14, Ambuye anati, “Koma Iye, m’mene adapereka nsembe imodzi cifuklwa ca macimo, anakhala pa dzanja lamanja la Mulungu cikhalire; kuyambira pomwepo alindirira, kufikira adani ace aikidwa akhale mpando ku mapazi ace. Pakuti ndi cipereko cimodzi anawayesera angwiro cikhalire iwo oyeretsedwa. ” Iye anati azayembekeza kufikira chiweruzo chomaliza kuti asankhe tsoka lawo.
Adani Ake akunenabe kuti, “Mulungu, chonde ndikhululukireni machimo anga.” Satana ndi otsatira ake sakhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndipo apitiliza kupempha chikhululukiro Chake.
Ambuye Mulungu wathu sazawaweruza pakali pano. Koma patsiku Lakubweranso Kwake Kwachiwiri, iwo adzaweruzidwa ndi kuponyedwa ku gehena kwamuyaya. Mulungu akuwalekerera kufikira tsiku limenelo mu chiyembekezo choti angalape ndi kukhala olungama kudzera mu chiombolo.
Ambuye wathu Yesu anachotsa machimo athu onse ndi kufa m’malo mwathu ife okhulupilira mwa Iye. Yesu tsiku lina azaonekera kachiwiri kuti aombole iwo onse amene akhulupilira mwa Iye. “O chonde bwerani kwa ife mwamsanga, Ambuye.” Iye adzabwera kachiwiri kuzatenga opanda uchimo kuti akhale ndi Iye kwamuyaya mu Ufumu wa Kumwamba.
Iwo amene akukakamira kuti adakali ochimwa pamene Ambuye adzabwerenso adzapeza kuti kulibe malo Kumwamba. Pa tsiku lomaliza, adzaweruzidwa ndi kuponyedwa ku moto wa gehena. Chilango chimenechi chikuyembekeza iwo amene akukana kukhulupilira mu kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.
Ambuye wathu Yesu amaona iwo amene akhulupilira mu chabodza ngati adani Ake. Ndi chifukwa chake tiyenera kumenyana ndi chabodzachi. Ndi chifukwa chake tiyenera kukhulupilira mu dalitso la uthenga wabwino wa kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.
TIYENERA KUKHULUPILIRA MU UTHENGA WABWINO WA MADZI NDI MZIMU
Kodi pali kufunika kwa chitetezero cha machimo athu tsopano popeza mphoto yathu ya (machimo) inalipiridwa kwanthunthu?
Ai, palibiletu.
Aheberi 10:15-16 anena kuti, “Koma Mzimu Woyeranso aticitira umboni; pakuti adatha kunena, ici ndi cipangano ndidzapangana nao, atapita masiku ajawo, anena Ambuye: ndidzapereka malamulo anga akhale pamtima pao; ndipo pa nzeru zao ndidzawalemba.’”
Atachotsa machimo athu onse, Iye anati “ici ndi cipangano ndidzapangana nao,.” Kodi pangano limeneli ndi lotani? “ndidzapereka malamulo anga akhale pamtima pao; ndipo pa nzeru zao ndidzawalemba.” Choyamba tinayesa kutsogoleredwa ndi moyo wazamalamulo mogwirizana ndi lamulo lake, koma sitingapulumutsidwe moona ndi lamulo.
Pambuyo pake tinadziwa kuti Yesu anapulumutsa kale iwo amene akhulupilira m’mitima yawo dalitso la uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Aliyense amene akhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu ndi owomboledwa.
Yesu ndi Ambuye wa chipulumutso. “” (Machitidwe a Atumwi 4:12). Yesu anabwera kudzikoli ngati Mpulumutsi. Chifukwa chakuti sitingapulumutsidwe kudzera mu ntchito zathu, Yesu anapulumutsa ife ndipo analemba pansi pa mitima yathu kuti Iye wapulumutsa ife ndi lamulo Lake la chikondi komanso chipulumutso.
“‘Ndipo macimo ao ndi masayeruziko ao sindidzawakumbukilanso. Koma pomwe pali cikhululukiro ca macimo palibenso copereka ca kwa ucimo. ” (Ahebri 10:17-18).
Tsopano Iye sakumbukilanso zochita zathu zolakwika. Tsopano popeza anachotsa machimo athu onse, ife okhulupirira tilibenso uchimo umene uyenera kukhululikidwa. Ngongole yathu inalipiridwa mwathunthu ndipo palibe china chotsala kuti chilipiridwe. Anthu akupulumutsidwa mwa chikhulupiliro mu utumiki wa Yesu, umene unapulumutsa ife kudzera mu ubatizo Wake ndiponso mwazi Wake pa Mtanda.
Tsopano chimene tiyenera kuchita ndi kukhulupilira m’madzi ndi mwazi wa Yesu. “Ndipo mudzazindikira coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani” (Yohane 8:32). Khulupilirani mu chipulumutso cha Yesu. Kupeza chiombolo ndi kosavuta kuposa kupuma. Chimene muyenera kuchita ndi kukhulupilira m’mene zinthu ziriri. Chipulumutso ndi kungokhulupilira m’mawu a Mulungu.
Khulupilirani kuti Yesu ndi Mpulumutsi wathu (mu ubatizo wa Yesu ndiponso imfa Yake pa Mtanda), ndipo khalani ndi chikhulupiliro chokha kuti chipulumutso ndi chanu. Kanani ndi maganizo a inu nokha ndipo khulupilirani mu chipulumutso cha Yesu. Ndi kupemphera kuti zoona mukhulupilire mwa Yesu ndipo mukonzeke kutsogoleredwa ku moyo osatha limodzi ndi Iye.