• All e-books and audiobooks on The New Life Mission website are free
  • Explore multilingual sermons in global languages
  • Two new revised editions in English have been released
  • Check out our website translated into 27 languages
Search

Sermons

Mutu 3: Uthenga Wabwino wa Madzi ndi Mzimu Woyera

[3-8] Ubatizo wa Yesu ndi NdondomekoYofunikira Kwambiri Pa chiombolo (Mateyu 3:13-17)

2021.05.22 115
Ubatizo wa Yesu ndi NdondomekoYofunikira Kwambiri Pa chiombolo(Mateyu 3:13-17)
“Pamenepo Yesu anacokera ku Galileya nadza ku Yordano kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye. Koma Yohane anati amkanize, nanena, Ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kw aine kodi? Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero. Pamenepo anamlola Iye. Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anaturuka m’madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye; ndipo onani, mau akucokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera. ”
 
 

UBATIZO WA YOHANE MBATIZI 


Kodi kulapa n’chiani?
Kutembenuka ku moyo wauchimo ndi kukhulupilira mwa Yesu pofuna kuyeretsedwa

Anthu ambiri m’dziko lino sadziwa chifukwa chimene Yesu anabwerera m’dzikoli komanso anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Motero tiyeni tinene za cholinga cha ubatizo wa Yesu ndiponso za Yohane Mbatizi amene anabatiza Iye. 
Choyamba, tiyenera kuganizira chimene chinapangitsa Yohane Mbatizi kubatiza anthu pa Yordano. Anafotokoza mu Mateyu 3:1-12 kuti Yohane Mbatizi anabatiza anthu kuti awabweretsenso kwa Mulungu kuchoka kumachimo mwa kuulula machimo awo. 
“Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima;” (ndime 11), ndiponso “Mau a wopfuula m’cipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zace’” (ndime 3). Yohane Mbatizi, anavala ubweya wa ngamira ndipo ananyamula mulu wa dzombe, nafuula m’chipululu, kulalikira ubatizo wa kulapa ku chikhululukiro cha machimo. 
Iye anafuula kwa anthu, “Lapani, Mpulumutsi wa mtundu wa anthu akubwera; konzani njira Yake, lungamitsani njira ya Ambuye ya chipulumutso. Siyani kupembedza milungu ya Anthu a mitundu ina ndipo landilani Ambuye mu mtima mwanu.”
Kubwerera ku chiani? Ku kupembeza mafano ndi zochita zonse zoipa za moyo wodzala ndi uchimo. Choncho n’chiani chimene tiyenera kuchita? Tiyenera kubatizidwa mwa Yesu kuti tiyeretsedwe. Yohane Mbatizi anafuula m’chipululu, “Batizidwani ndi ine. Khalani otsukidwa ku machimo anu. Mpulumutsi, Mesiya wanu, akubwera kudzikoli. Azanyamula machimo anu onse monga Mwana wankhosa operekedwa nsembe wa mu Chipangano Chakale ndi kutsuka machimo anu onse.” 
Mu Chipangano Chakale, machimo a masiku onse ankaperekedwa ku nsembe yauchimo kudzera mu kuika manja. Machimo a pa chaka a Israyeli onse naonso ankaperekedwa pa mbuzi ndi mkulu wansembe pa Tsiku la chitetezero cha machimo, limene linagwera pa tsiku la khumi la mwezi wa chisanu ndi chiwiri chaka chilichonse (Levitiko 16:29-31). 
M’njira yomweyo, machimo a mtundu wa anthu anayenera kuperekedwa kwa Yesu kudzera mu ubatizo Wake kamodzi kokha kuti afafanizidwe kudzera mwa Iye. Choncho Yohane anachenjeza anthu kuti abwerenso kwa Yesu ndipo abatizidwe ndi iye. 
Chofunika kwambiri cha ubatizo anachita Yohane Mbatizi chinali kulapa. Umene unabweretsanso anthu a Israyeli kwa Yesu amene anali nkudza patsogolo pake. Kulapa kukutanthauza kutembenuka ku moyo wa uchimo ndi kukhulupilira mwa Mesiya pofuna kukhululukidwa ku machimo onse. 
Anthu a ku Israyeli akanaomboledwa poyembekezera Mesiya amene adzabwere posachedwa kuti atsuke machimo awo onse. Chimodzimodzi, timaomboledwa mwa kukhulupilira mwa Yesu, amene anatsika kuchoka Kumwamba zaka zikwi ziwiri (2000) zapitazo ndi kutsuka machimo onse a dziko. Koma Israyeli mu Chipangano Chakale ananyalanyaza lamulo la Mulungu, ankapereka nsembe zolakwika ndipo anaiwala Mesiya. 
Popeza Yohane Mbatizi ankayenera kuwakumbutsa za lamulo la Mulungu ndiponso za Mesiya amene ali nkudza patsogolo pake, anayamba kubatiza anthu ndipo pamenepo anabatizanso Yesu pa Yordano. 
Anthu ambiri anadza kwa Yohane ndipo anabatizidwa, analapa ku kupembeza kwa mafano ndi kunyalanyaza lamulo la Mulungu. Pali zinthu zitatu zofunika kwambiri mu kaperekedwe ka nsembe yoyenera―nyama yamoyo, kuika manja, ndi mwazi wake. Anthu onse a m’dziko apulumutsidwa mwa kukhulupilira mwa Yesu. 
Pamene Afalisi ndi asaduki anadza kudzabatizidwa, Yohane anafuula kwa iwo, “Obadwa a njoka inu, ndani anakulangizani kuthawa mkwiyo ulinkudza? Onetsani inu zipatso zakuyenera kutembenuka mtima: ndipo musamayesa kunena mwa inu nokha, Atate wathu tiri naye Abrahamu” (Mateyu 3:7-9).
Afalisi ndi asaduki amenewa anali magulu a ndale ndiponso opembeza-mafano, amaganiza kuti ndi anthu a Mulungu kupatula zoona zoti sankakhulupilira m’mawu a Mulungu. Iwo ankakhulupilira mwa milungu ina ndi mwa maganizo a iwo okha. 
Pamene anabwera kwa Yohane Mbatizi kuti abatizidwe, iye anawauza kuti, “Musamapereke nsembe zolakwika koma tembenukani ku uchimo ndipo moona khulupilirani kuti Mesiya adzabwera kudzatsuka machimo anu. Muyenera kukhulupilira zimenezi mu mitima yanu.” 
Kulapa ndi kutembenuka ku njira yoipa. Kulapa koona ndi kutembenuka ku uchimo ndi zikhulupiliro zabodza ndi kubwera kwa Yesu. Ndi kukhulupilira mu chiombolo cha ubatizo Wake ndi chiweruzo Chake cha pa Mtanda. 
Motero, Yohane Mbatizi anapfuula ku anthu a Israyeli, amene anasiya lamulo la Mulungu ndi ndondomeko ya kaperekedwe ka nsembe, ndi cholinga choti awanyengerere abwerere kwa Mulungu. Inali ntchito ya Yohane Mbatizi kubweza anthu kubwera kwa Yesu kotero kuti akhulupilire mwa Iye ndi kupulumutsidwa ku machimo awo onse.
 
 

KODI MUMAKHULUPILIRA M’CHIOMBOLO KUDZERA MU UBATIZO WA YESU?

 
Kodi anthu onse ayenera kuchita chiani pamaso pa Yesu?
Ayenera kukhulupilira mwa Iye kuti apulumutsidwe ku machimo awo onse.

Chinthu choyamba chimene Yesu anachita pa utumiki Wake wapoyera ndi kubatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Machimo onse a dziko anaperekedwa pa Iye m’njira imeneyi. 
Motero ubatizo wa Yesu unali chiyambi cha chipulumutso cha Mulungu kwa mtundu wa anthu komanso ntchito ya chilungamo ya Yesu imene inatsuka machimo onse a dziko. Mulungu anaombola onse amene akhulupilira mu choonadi kuti Yesu anachotsa machimo onse a dziko kudzera mu ubatizo Wake. 
Pamene Yesu anabwera kudzikoli ndi kubatizidwa ndi Yohane Mbatizi, uthenga wabwino wa Ufumu wa Kumwamba unayambika. Miyamba inatseguka ndi ubatizo Wake ndipo monga anafotokozera mu Mateyu 3:15, chinali ngati nsembe ya chitetezero cha machimo inafotokozedwa mu Levitiko 1:1-5, 4:27-31 mu Chipangano Chakale. 
Zonse za mu Chipangano Chakale zili ndi zinzake mu Chipangano Chatsopano ndipo mobwerezabwereza. “Funani inu m’buku la Yehova, nimuwerenge; palibe umodzi wa iye udzasowa, palibe umodzi udzasowa unzace” (Yesaya 34:16).
 
 

CHIPANGANO CHAKALE NDI CHIPANGANO CHATSOPANO ZONSE ZIKUNENA ZA CHITETEZERO CHA MACHIMO A ANTHU ONSE

 
Kodi tiyenera kulapa masiku onse chifukwa cha machimo athu a tsiku ndi tsiku?
Ai. Kulapa koona ndi kuvomereza machimo onse a munthu ndi kutembenuza maganizo a munthu ku ubatizo wa Yesu pofuna kupeza chiombolo.
 
Mu Chipangano Chakale, uchimo wa tsiku limodzi unali kuperekedwa ku nsembe yauchimo mwa kuika manja. Nsembe ija kenako inkakhetsa mwazi ndi kuweruzidwa m’malo mwa ochimwa. Ndiponso machimo onse amene ankachitika pa chaka anali kuperekedwanso pa nsembe yauchimo mwa kuika manja, kuti anthu onse akhululukidwe ku uchimo wa pa chaka. 
Mu Chjipangano Chatsopano, mwa njira imodzimodzi, Yesu Kristu anabwera ndipo anabatizidwa pa Yordano kuti achotse machimo onse a dziko. Mwa ichi mawu a Mulungu amene ananenedwa mu Chipangano Chakale anakwaniritsidwa. 
Yohane Mbatizi, amene anabatiza Yesu, anali mtumiki wa Mulungu amene anatumizidwa miyezi isanu ndi umodzi patsogolo pa Yesu. Iye anachitira umboni kuti Yesu anachotsa machimo onse adziko, ananena mu Yohane 1:29. “Onani mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” 
Yohane Mbatizi anapereka machimo a dziko pa Yesu mwa kubatiza Iye pa Yordano. Mwa njira imeneyi, Ambuye anapanga chitetezero cha machimo onse a mtundu wa anthu. Chimene tiyenera kuchita tsopano ndi kukhulupilira. 
Machimo onse a dziko anaperekedwa pa Yesu. Ophunzira a Yesu anati mu Macitidwe a Atumwi 3:19, “Cifukwa cace lapani, bwererani kuti afafanizidwe macimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zocokera ku nkhope ya Ambuye.” 
Iwo anali kuchenjeza ife kuti timvetsetse chifukwa chimene Yohane anabatiza Yesu, chifukwa chimene ankauzira anthu kuti atsatire Iye. Iye anati, “Lapani ndipo khalani osinthidwa. Khulupilirani mu chiombolo cha ubatizo wa Yesu. Khalani otsukidwa ku machimo anu.” 
Mesiya anabwera ndi kutsuka machimo athu onse pa nthawi imodzi mwa kubatizidwa. Machimo onse a dziko anaperekedwa kwa Yesu mwa njira imeneyi. Motero Pangano la Mulungu linakwaniritsidwa ndi ubatizo wa Yesu, monga analembera mu Mateyu 3:13-17. 
“Pamenepo Yesu anacokera ku Galileya nadza ku Yordano kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye. Koma Yohane, anati amkanize, nanena, ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi? Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero. Pamenepo anamlola Iye. Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anaturuka m’madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye; ndipo onani, mau akucokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.” 
Kuti akwaniritse chipulumutso cha Mulungu, Yesu anadza kwa Yohane Mbatizi kuti abatizidwe. Yohane M’batizi anali mtumiki wapadera kwambiri wa Mulungu. Luka ndime yoyamba akunena kuti Yohane anali mbeu ya Aroni, mkulu wansembe oyamba. Mulungu anasankha Yohane, mbeu ya Aroni, chifukwa ankafuna oyimira mtundu wa anthu kuti akwaniritse chilungamo chonse. 
Choncho, Mulungu anapanga Yohane kubadwa m’nyumba ya mkulu wansembe miyezi 6 Yesu asanabadwe. Yohane Mbatizi anakonza njira ya Yesu mwa kupfuula ku chipululu, “Lapani, inu obadwa a njoka! Lapani ndipo musinthidwe. Mesiya akubwera. Khalani osinthika kwa Iye, kapena adzakudulani ndi kukuponyani ku moto. Khulupilirani mu ubatizo Wake ndi mwazi Wake pa Mtanda. Lapani ndipo batizidwani, ndiyeno mudzaomboledwa.” 
Uthenga wabwino wa chiombolo ukufotokozedwa poyera mu Machitidwe 3:19. Pamene Yohane Mbatizi anapfuula za machimo a mtundu wa anthu, ambiri anasinthidwa. 
Chifukwa Yohane anapereka machimo a dziko kwa Yesu, machimo onse a mtundu wa anthu anachotsedwa panthawi imodzi. Chifukwa chakuti Yohane M’batizi ananenera kuti Yesu anayamula machimo athu onse, tikudziwa kuti tingapulumutsidwe mwa kukhulupilira mu uthenga wabwino wa chiombolo, uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
 
 

CHIFUKWA CHIMENE YOHANE MBATIZI ANAYENERA KUBWERA YESU ASANABWERE

 
Kodi “Motero” akutanthauzanji?
1) Chabwino kwambiri 
2) Choyenera kwambiri
3) Chofunika m’njira iyi yokha 
(palibe njira ina)

Iwo amene machimo awo anatsukidwa mwa kukhulupilira Yesu, Mpulumutsi, angatsimikize chipulumutso chawo kudzera mu umboni wa Mateyu ku uthenga wa ubatizo wa Yesu. Mu Mateyu 3:15-16, Yesu anabwera kwa Yohane ndi kunena kuti, “Ndibatize Ine.” Ndipo Yohane anayankha kuti, “Ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu mudza kwa ine kodi?” 
Anali Yohane Mbatizi amene anabatiza Yesu, anazindikira m’mene Iye analili. Yohane anali mtumiki wa Mulungu amene anatumizidwa kuti apereke machimo onse a mtundu wa anthu pa Yesu. Chifukwa chakuti Yesu anadza ngati Mpulumutsi kuzakwaniritsa uneneri wa m’Chipangano Chakale, Iye analamula Yohane Mbatizi kuti amubatize kotero kuti anyamule machimo onse adziko pamutu Pake. 
Chifukwa chiani? Chifukwa chakuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu Wamphamvu yonse, Mlengi, ndiponso Mpulumutsi. Iye anabwera kwa ife kuti atsuke machimo athu onse. Choncho, kuti apulumutse anthu onse, Iye anayenera kubatizidwa. 
“motero” Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi ndi kutsuka machimo athu onse. Iye anaweruzidwa m’malo mwathu pa Mtanda. Ubatizo wa Yesu unali umboni wa chipulumutso chathu. Monga m’mene Mulungu analonjezera mu Chipangano Chakale kuti machimo onse a dziko adzaperekedwa ku nsembe ya Mwana wankhosa. Mwana wa Mulungu anakhala Mwana wankhosa ndi kunyamula machimo athu onse pa Iye yekha. 
Choncho zonse kuika manja kwa mu Chipangano Chakale ndiponso ubatizo wa Yesu wa mu Chipangano Chatsopano ndi kuperekedwa kwa machimo, ndipo chipulumutso ndi moyo osatha zikuperekedwa kwa iwo amene akhulupilira mu uthanga wabwino wa madzi ndi Mzimu. 
 
 

UBATIZO WA YESU UNATSUKA MACHIMO ATHU ONSE 


Kodi tingavale bwanji Kristu?
Mwa kubatizidwa mwa Kristu

Pamene Yesu ankafuna kubatizidwa, Yohane anayesa kumuletsa ponena kuti, “Ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi?” 
Koma Yesu anayankha nati, “Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero.” Balola tsopano. Balola. Iye anauza Yohane, “Uyenera kupereka machimo a anthu onse kwa Ine kuti ndibweretse kwa Ine onse amene akhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi wa chiombolo. Ndiyeno ndizaweruzidwa chifukwa cha machimo awo kotero kuti onse amene akhulupilira mu ubatizo Wanga adzaomboledwe ku machimo onse. Pereka kwa Ine machimo a dziko kudzera mu ubatizo kuti onse amene dzabwere patsogolo panga adzaomboledwe ku machimo awo pa nthawi imodzi. Choncho balola tsopano.” 
Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi ndipo ubatizo wa Yesu unali mogwirizana ndi chilungamo cha lamulo la chiombolo cha Mulungu. Chifukwa chakuti machimo onse anaperekedwa pa Yesu pamene anabatizidwa, tingaomboledwe pa nthawi imodzi pamene takhulupilira mwa Yesu ndipo tabatizidwa. Chifukwa chakuti ananyamula machimo athu onse kudzera mu kuika manja, kufa pa Mtanda m’malo mwa ife ndipo tsopano akukhala kudzanja lamanja la Mulungu, tingapulumutsidwe mwa kukhulupilira mu chiombolo cha madzi ndi Mzimu. 
Iye ndi Yesu, amene anatipulumutsa ife ku machimo onse adziko. Tingapulumutsidwe mwa kukhulupilira kuti Yesu ananyamula machimo athu onse ndipo analipira mphotho ya machimo athu onse pa Mtanda. Ubatizo wa Yesu unali chiyambi cha uthenga wabwino wachiombolo. 
Ubatizo wa chiombolo umatchulidwa kwambiri mu Baibulo ndipo mtumwi Paulo nayenso ananenapo mu Agalatiya kuti anapachikidwa pamodzi ndi Kristu chifukwa anabatizidwa mwa Kristu ndi kuvala Kristu. Mtumwi Paulo ananenapo za chikhulupiliro cha chiombolo kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi imfa Yake ya pa Mtanda. 
 

“BALOLA TSOPANO”

Kodi ntchito ya Yohane Mbatizi inali yotani?
Ntchito yake inali yopereka machimo onse a dziko kwa Yesu ngati mkulu wansembe wa mtundu wa anthu.

Yesu anati, “pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero.” Chilungamo chonse chikutanthauza kuchotsa machimo onse kudzera mu ubatizo Wake ndi kupanga anthu onse kukhala opanda tchimo m’mitima yawo. “Pomwepo anamlola Iye.” Yesu anabatizidwa pa Yordano. 
Monga m’mene mkulu wansembe ankaikira manja ake pa mutu pa mbuzi, Yohane Mbatizi anaika manja ake pa mutu pa Yesu ndi kupereka machimo onse a dziko pa Iye. Yohane Mbatizi anali mkulu wansembe amene ntchito yake inali yopereka machimo onse a dziko pa Yesu ngati oyimilira wa anthu. “Mulungu, ndikupereka machimo onse a dziko pa Mwana wa nkhosa Wanu, Yesu.” Motero machimo onse a dziko anaperekedwa pa Yesu. 
Yohane Mbatizi anaika manja ake pamutu pa Yesu, ndikumumiza m’madzi, ndiyeno anachotsa manja ake pamene Yesu anaturuka m’madzi. Ubatizo wa Yesu unapangidwira chipulumutso cholungama. Motero Yesu anapulumutsa mtundu onse wa anthu amene akhulupilira mu ubatizo Wake. 
 

KUMWAMBA KUNATSEGUKA NDIPO MAWU ANAMVEKA KUCHOKERA KUMWAMBA 

N’kuchokera nthawi iti pomwe ufumu wa Kumwamba unatseguka?
Kuchokera m’masiku a Yohane Mbatizi (Mateyu 11:12)

“Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anaturuka m’madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye; ndipo onani, mau akucokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.” (Mateyu 3:16-17).
Pamene Yesu ananyamula machimo onse a dziko ndi ubatizo Wake, miyamba inamtsegukira Iye. Motero pangano la Mulungu limene linapangidwa zaka masauzande ambirimbiri kale kalelo linakwaniritsidwa kudzera mu ubatizo wa Yesu pa Yordano. 
Motero Yesu, ngati Mwana wa nkhosa wa Mulungu, anapulumutsa anthu onse a dziko ku machimo awo. Machimo onse adziko anaperekedwa pa Yesu ndipo Iye anakwaniritsa chifuniro cha Mulungu. 
Anachitira umboni mu Yohane 1:29, “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” Chifukwa chakuti machimo onse anaperekedwa pa Yesu, Mwana wa nkhosa wa Mulungu, Iye anayenda molunjika Mtanda pa Golgota patatha zaka zitatu ndi chisautso pa mapewa Pake. Pamene anachotsa machimo onse ndi ubatizo Wake, kulikonse kumene anali kupita, ankauza iwo amene anamulandira mwa chikhulupiliro kuti machimo awo onse akhululukidwa. 
Mu Yohane 8:11, Anauza mkazi amene anagwidwa chigololo, “Inenso sindikutsutsa iwe” Iye sanathe kumutsutsa chifukwa chakuti munthu amene ankayenera kuweruzidwa anali Yesu Iye yekha, amene anatenga uchimo onse. Motero anauza anthu onse kuti Iye anali Mpulumutsi wa ochimwa. 
Chifukwa Iye, Mwana wa Mulungu, anachotsa machimo athu onse, okhulupilira aliyense m’dziko angakhale oyeretsedwa. Miyamba inatseguka pamene Iye anali kubatizidwa. Zipata za Ufumu wa Kumwamba zinatseguka ndipo iye amene akhulupilira mu ubatizo wa Yesu angalowe momasuka.
 
 

YESU ANAPACHITIKDWA PAMENE ANACHOTSA MACHIMO ONSE A DZIKO KUDZERA MU UBATIZO WAKE 

 
Kodi Yesu anaponda bwanji Mutu wa Satana?
Mwa kuukanso kwa akufa atavomereza chiweruzo cha machimo athu onse

Chifukwa chakuti machimo onse anaikidwa pa mutu Pake, Yesu anayenera kuweruzidwa pa Mtanda. Iye anali wachisoni kwambiri ndiponso ovutika mtima pamene ankaganizira za masautso omwe adzapitamo pa Mtanda. Iye anapemphera kufikira thukuta Lake linakhala monga madontho a mwazi. Pamene anapita limodzi ndi ophunzira Ake ku malo otchedwa Getsemani, Iye analira, “Atate, ngati nkutheka, cikho ici cindipitirire Ine” (Mateyu 26:39). “Ndibabatizidwa ndipo ndinanyamula machimo onse a dziko, koma musalole Ine kuti ndife nawo.” Koma Mulungu sanayankhe. 
Pa Tsiku Lachitetezero cha machimo mu Chipangano Chakale, nsembe yauchimo inkayenera kuphedwa kotero kuti mwazi wake uwazidwe pamaso pa mpando wachifundo ndi mkulu wansembe. Mwa njira imodzimodzi, Yesu anayenera kupachikidwa ndipo Mulungu anaona kuti angachite popanda njira ina iliyonse. 
Guwa ndi chiweruzo cha Mulungu ndipo mwazi wa nsembe yauchimo ndi moyo. Kuwaza mwazi kasanu ndi kawiri kuno ndi uko patsogolo pa mpando wachifundo kukutanthauza kuti chiweruzo chonse chinaperekedwa (Levitiko 16:1-22). 
Yesu anapemphera kwa Mulungu kuti chikho cha masautso chimupitilire. Koma Atate Wake sanavomereze ndipo Yesu pomaliza anati, “koma si monga ndifuna Ine, koma Inu” (Mateyu 26:39). Anapemphera kwa Mulungu kuti achite m’mene Iye akuonera kuti ndi kwabwino. Anamaliza kupemphera ndi kutsatira chifuniro cha Atate Wake. 
Yesu anapereka chifuniro Chake ndi kumvera Atate Wake. Chifukwa chiani? Chifukwa chakuti ngati sakanaweruzidwa pambuyo pa kunyamula machimo a dziko, chipulumutso sichikanamalizika. Iye anapachikidwa chifukwa chakuti ananyamula machimo a mtundu wa anthu kudzera mu ubatizo Wake. “Pakuti mphotho yace ya ucimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu” (Aroma 6:23).
Mulungu anakwaniritsa pangano limene likunena kuti adzatuma Mpulumutsi ndi kupulumutsa anthu kudzera mu kuika manja, ubatizo wa Yesu. Yesu anamvera chifuniro cha Mulungu ndipo anavomereza chiweruzo m’malo mwa ife. 
Ndiponso ndi kukwaniritsidwa kwa uneneri wa mu Genesis 3:15, “Ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yace; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira citende cace.” Mulungu analonjeza Adamu kuti azatuma Mesiya, mbeu ya Hava, ndipo idzagonjetsa mphamvu ya Satana imene inapangitsa mtundu wa anthu kuchimwa ndi kupita ku gehena. 
Pamene tikudziwa ndi kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi imfa Yake ya pa Mtanda, machimo athu onse anatsukidwa ndipo tinapulumutsidwa ku chiweruzo. 
Tiyenera kukhala ndi chikhulupiliro chomveka m’mitima yathu pamene tikuvomereza ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda. Khulupilirani zimenezi m’mitima yanu, ndipo mudzapulumutsidwa.
 
 

UBATIZO WA YESU NDI CHIYAMBI CHA UTHENGA WABWINO WA KUMWAMBA

 
Kodi lamulo lomaliza la Ambuye ndi lotani asanakwere Kumwamba?
Analamula ophunzira Ake kuti apange ophunzira a maiko onse pobatiza m’dzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Oyera.

Ubatizo wa Yesu unali chiyambi cha uthenga wabwino, ndipo Iye anapulumutsa ochimwa onse ndi ubatizo Wake komanso mwazi. Mu Mateyu 28:19, kunalembedwa kuti, “Cifukwa cace mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera.” Yesu anauza ophunzira Ake kuti achitire umboni kuti Atate ndi Mwana komanso Mzimu Oyera anapulumutsa mtundu onse wa anthu ku machimo awo ndi kuwatsuka onse kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi Wake. 
Yesu anawapatsa mphamvu yopanga ophunzira a mitundu yonse, kuwaphunzitsa za ubatizo wa Yesu, ubatizo wa chiombolo, ubatizo umene unatsuka machimo onse adziko. 
Pafupifupi zaka zikwi ziwiri (2000) zapitazo, Yesu anabwera pa dziko lapansi m’thupi ndipo anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Ndi ubatizo wa Yesu, machimo onse adziko, kuphatikizapo machimo athu onse, anaperekedwa pa Iye. 
Kodi ndi machimo angati amene anaperekedwa kwa Iye? Kodi za machimo a mawa ziri bwanji? Iye anatiuza kuti ngakhalenso machimo a mawa anaperekedwa pa Iye. Machimo a ana athu, aja a mbadwo onse, akale atsopano ndi akutsogolo, ngakhale aja a Adamu anaperekedwa kwa Yesu. 
Kodi kungakhale bwanji kulibe uchimo? Kodi ife tingakhale bwanji tilibe uchimo? Chifukwa chakuti Yesu anachotsa machimo athu onse ndi machimo onse a dziko ndi ubatizo Wake kuti okhulupilira onse amasuke okha ku uchimo ndi kupeza njira ya ku Ufumu wa Kumwamba. 
“Koma wocita coonadi adza kuunika, kuti nchito zace zionekere kuti zinacitidwa mwa Mulungu.” (Yohane 3:21). 
Yesu anatsuka machimo athu onse ndi ubatizo Wake, mwazi Wake pa Mtanda, imfa Yake, ndi kuukanso Kwake. Motero kukhulupilira mu ubatizo Wake ndi imfa Yake ya pa Mtanda ndi kupulumutsidwa ku uchimo onse. Ichi ndi chikhulupiliro cha chiombolo. 
Pamene takhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Kristu, ndife opulumutsidwa. Ngati tikhulupilira mwa Yesu molondola, kodi ndife olungama kapena ochimwa? Ndife olungama. Kodi tilibe uchimo ngakhale kuti ndife anthu operewera? Inde, ndife opanda tchimo. Kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi chiweruzo Chake cha pa Mtanda ndiko kukhala ndi chikhulupiliro chabwino komanso chanthunthu.
 
 
KUBATIZA NDI KUBATIZIDWA M’DZINA LA YESU 

Kodi chiyambi cha uthenga wabwino wakumwamba ndi chiani?
Ubatizo wa Yesu

Chifukwa chakuti anthu ndi operewera, atumiki amabatiza aja amene akhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake kuti awapange alimbitse chikhulupiliro chawo. Obadwa mwatsopano amaonetsetsa kuti anapulumutsidwa mwa kubatizidwa mwa njira imodzi ya ubatizo wa Yesu ngati umboni wa chikhulupiliro. 
Mtumiki choyamba amapemphera manja ake ali pamutu pa munthu obadwa mwatsopano, kupempha dalitso la Mulungu kuti munthu ameneyu amupembeze bwino kufikira kumapeto kwa masiku ake. Ndiyeno amamubatiza m’dzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Oyera. 
Timabatizidwa chifukwa cha chikhulupiliro chathu mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Ubatizo umenewu ndi owonetsa kuti uchimo onse unaperekedwa pa Yesu, kuti munthu obatizidwa anafa limodzi ndi Yesu ndipo anaukitsidwanso limodzi ndi Iye. 
Kubatizidwa ndi kuulula chikhulupiliro cha munthu mu kupereka kwa machimo pa Yesu kudzera mu ubatizo Wake, mu kuweruzidwa chifukwa cha machimo a munthu pamodzi ndi Yesu ndiponso mu kuukitsidwa pamodzi Naye. Ndi kuulula chikhulupiliro cha munthu pamaso pa Atate, Mwana, ndi Mzimu Oyera, Satana komanso kwa abale ndi alongo. Ndi kuulula kuti munthu wabadwanso mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. 
Kwa iwo amene akhulupilira mwa Yesu, akudziwa tanthauzo loona la ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda, anapulumutsidwa ku machimo onse a dziko. Motero anabatizidwa mwa dzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Oyera. 
“Zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.” (2 Akorinto 5:17). Zinthu zathu zakale zapita ndipo tinabadwa mwatsopano ngati anthu achikhulupiliro. Kuti titsimikize mu mitima yathu, tinabatizidwa. Tinabatizidwa mwa Yesu mwa kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu. 
 

MOYO PAMBUYO PA KUBADWA MWATSOPANO MWA UBATIZO WA YESU NDI MWAZI WAKE PA MTANDA 

Kodi obadwa mwatsopano akukhalira chiani?
Akukhalira ufumu wa Mulungu ndi chilungamo Chake, kulalikira uthenga wabwino padziko lonse lapansi.

Moyo pambuyo pa kuomboledwa ndi kubadwanso mwatsopano uyenera kukhudza chikhulupiliro m’mawu a Mulungu. Suyenera kukhala moyo wachisoni umene munthu ayenera kulapa machimo ake a masiku onse. Koma, uyenera kukhala moyo wachikhulupiliro umene tikutsimikiza kuti Yesu anachotsa machimo athu onse ndi ubatizo Wake. 
Machimo athu onse anaperekedwa pa Yesu pamene anabatizidwa. Ndiyeno Iye anakhala zaka zitatu ndi cholemetsa chimenechi kufikira pamene anavomereza chiweruzo cha machimo athu onse ndi kupachikidwa. 
Motero ife okhulupilira tiyenera kukhala ndi chikhulupiliro mu mawu olembedwa, osati mu zochitika chabe. Ngati tilephera kuchita choncho, tidzayamba kudandaula za machimo athu a masiku onse pambuyo pakuti tinaomboledwa ndi kubadwa mwatsopano. 
Tiyenera kuchotsa nkhani ya uchimo ndi kukhulupilira kokha mu uthenga wabwino wa madzi ndi mwazi. Uwu ndi moyo umene owomboledwa ayenera kukhala nawo. 
Kodi Yohane Mbatizi ananena chiani za Yesu? Iye anati, “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” (Yohane 1:29). Iye anachitira umboni kuti Yesu anachotsa machimo a lero, mawa, ndi adzulo, onse kufikira ku tchimo loyamba. 
Kodi Iye sanachotse machimo onse amenewo? Kodi machimo amenewo sanaperekedwe pa Yesu? tchimo la dziko likuphatikizapo machimo athu onse akale, atsopano, ndi amene ali kutsogolo. Tiyenera kutsimikiza za uthenga wabwino wa chiombolo kudzera mu ubatizo wa Yesu. 
Iwo amene akukhulupilira mu choonadi cha ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake adzapulumutsidwa. Aliyense amene akhulupilira mu ubatizo wa Yesu alibe tchimo mu mtima mwawo. 
Komabe, anthu ambiri akuganiza kuti adakali ndi uchimo chifukwa chakuti sakudziwa kuti machimo awo onse anaperekedwa kale pa Yesu kudzera mu ubatizo Wake. Iwo amanyengedwa ndi Satana. Satana akuwanong’oneza kudzera mu maganizo awo a thupi. “Mumachimwa masiku onse. Kodi mungakhale opanda uchimo?” 
Ayenera kokha kukhulupilira mwa Mulungu kuti akhale opanda uchimo. Palibe yemwe ali ndi uchimo ngati iye akhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda. 
Chifukwa chakuti tikukhala m’dzikoli ngati operewera ndiponso anthu ofoka, sitinganene kuti timakhala olungama kudzera mu ntchito zathu ndi zochita zokha. Koma tinganene ndi chikhulupiliro kuti tinapulumutsidwa ndi choonadi cha ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda. Tikangozindikira kuti mwa kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, mitima yathu imakhala yoyeretsedwa, timadziwa bwino kuti tilibe uchimo. 
“♬ Ndinaomboledwa. Munaomboledwa. Ife tonse tinaomboledwa ♬” Ndi chinthu chochititsa chimwemwe ndiponso chosangalatsa kukhala mwa chikhumbo chofuna kulalikira uthenga wabwino kwa onse ndiponso kudziwa kuti tikutsogoleredwa mwa Mzimu. 
Indedi ife okhulupirira timachimwa masiku onse koma tilibe uchimo. Tili ndi ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake m’mitima yathu. Mitima yathu inali kudzala ndi uchimo, koma tsopano popeza tikukhulupilira mu ubatizo wa Yesu, kodi tingakhalebe ndi uchimo bwanji. 
“Ici ndi cipangano ndidzapangana nao, atapita masiku ajawo, anena Ambuye: ndidzapereka malamulo anga akhale pamtima pao; ndipo pa nzeru zao ndidzawalemba,” (Aheberi 10:16).
Mitima yathu ndiyomasuka ku uchimo. Yesu anakwanitsa kutiombola kwanthunthu ndi ubatizo Wake ndiponso imfa Yake ya pa Mtanda. Chipulumutso cha uchimo chichokera ku chikhulupiliro mu mawu a Mulungu. 
 

ALIYENSE AMENE AKHULUPILIRA MU UBATIZO WA YESU NDI MWAZI WAKE PA MTANDA SANGAKHALENSO OCHIMWA 

Kodi timakhalanso ochimwa pamene tachimwa?
Ai, sitimakhalanso ochimwa

Pamene sitikukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, zilibe kanthu kuti tinkapemphera motani chikhululukiro, munali uchimo mu mitima yathu. Koma pamene tinayamba kukhulupilira mu uthenga wabwino oona, machimo athu onse anatsukidwa. 
“Inu, zatheka bwanji kuti muziwala ndi kusangalala masiku ano?” 
“Mukuona, ndilibenso uchimo mu mtima mwanga.” 
“Zoonadi? Ndiyeno ndikuganiza kuti mungachimwe m’mene mukufunira tsopano?” 
“Mukudziwa, munthu sangadzithandize koma kuchimwa. Umo ndi m’mene munthu alili. Koma Yesu anachotsa machimo onse ndi ubatizo Wake ndi kuvomereza chiweruzo m’malo mwawo pa Mtanda. Pa chifukwa ichi tsopano ndikuzipereka ndekha pa kutumikira uthenga wabwino mu mpingo. Aroma 6 akunena kuti ife tonse tiyenera kukhala motere. Popeza ndilibenso uchimo mu mtima mwanga,ndikufuna kuchita chinthu cholungama. Tiyenera kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda ndi kulalikira uthenga wabwino kuzungulira dziko lonse lapansi! Pamene tikhulupilira mwa Yesu, Mbuye wathu wachiombolo, sitingakhalenso ochimwa. Tiyenera kukhulupilira mu chipulumutso chosatha cha ubatizo wa Yesu ndi cha mwazi Wake pa Mtanda. Ndine odzala ndi chiyamiko chachikulu!”
 
 

NDANI AMALANDIRA MZIMU? 


Kodi Yohane Mbatizi ananena chiani za Yesu?
Anachitira umboni kuti Yesu anali mwana wankhosa wa Mulungu amene anachotsa machimo onse a dziko, otchedwa, machimo akale, atsopano ndi  amtsogolo, ngakhalenso tchimo loyamba

Aliyense amene wakhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda walandira chipulumutso. Kodi timalandira bwanji Mzimu? Machitidwe a Atumwi 2:38-39 akutiuza yankho. “Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu, m’dzina la Yesu Kristu kuloza ku cikhululukiro ca macimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. Pakuti lonjezano liri kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi onse akutali, onse amene Ambuye Muliungu wathu adzaitana.’”
Kubatizidwa m’dzina la Yesu Kristu kukutanthauza kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi kuomboledwa. Ndiyeno Mzimu uzapatsidwa ngati mphatso kuchokera kwa Mulungu. 
Kubatizidwa m’dzina la Yesu Kristu kukutanthauzanso kukhala oyeretsedwa mwa kukhulupilira mu ubatizo wa Kristu ndi mwazi. Pamene tikuchengeta chikhulupiliro chimenechi, timakhala owomboledwa ndipo timakhala olungama. Okhulupilira amakhala oyera ngati matalala kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda. 
“Ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.” Pamene takhulupilira molimba kuti machimo athu onse anaperekedwa pa Yesu kudzera mu ubatizo wa Wake ndiponso kuti anaweruzidwa chifukwa cha iwo pamodzi ndi imfa Yake pa Mtanda, mitima yathu imatsukidwa kukhala yoyera. Miyoyo yathu yatsopano imayamba pamene takhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake ndi kulandira mphatso ya Mzimu Woyera ndi kukhala ana a Mulungu. 
“Ndipo mudzazindikira coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani” (Yohane 8:32). Tiyenera kudziwa tanthauzo lenileni la chiweruzo cha Ambuye pa Mtanda. Choonadi ndi chakuti Yesu anachotsa machimo athu onse ndi ubatizo Wake ndiponso imfa Yake ya pa Mtanda. Chiombolo chimaperekedwa kwa ife pamene takhulupilira choonadi. 
 
 

UBATIZO WA YESU UNAOMBOLA IFE 


Kodi ndani amalandira Mzimu?
Iye amene waomboledwa ku uchimo onse kudzera m’chikhulupiliro cha mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda

Chitetezero cha machimo kudzera mu ndondomeko yakaperekedwe ka nsembe mu Chipangano Chakale chikuimilira ubatizo wa Yesu mu Chipangano Chatsopano. Ubatizo wa Yesu ndi mtima wa uneneri onse wa m’Chipangano Chakale. Cholingana ndi kuika manja mu Chingano Chakale chikupezeka mu ubatizo wa Yesu mu Chipangano Chatsopano. 
Machimo onse a dziko anaperekedwa pa Yesu kudzera mu ubatizo Wake monga m’mene machimo a Israyeli ankaperekedwa pa mbuzi yamoyo kudzera mu kuika manja. 
Kodi tiyenera kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu kuti tipulumutsidwe ku machimo athu onse? Inde! Titero! Tiyenera kuvomereza choonadi cha kuti Yesu anachotsa machimo onse a dziko kudzera mu ubatizo Wake. Ngati sitikhulupilira mu ubatizo wa Yesu, machimo athu sangaperekedwe pa Iye. Tiyenera kukhulupilira choncho kuti tipange chipulumutso chathu kukhala chanthunthu. Ngati sititero, sitingakhale olungama. 
Yesu anapulumutsa ochimwa onse a dziko mwa njira yoyenera ndiponso yachilungamo ndi ubatizo Wake. Sikanachitika mwa njira yoyenera kwambiri. Chifukwa chakuti ubatizo wa Yesu unali njira imene machimo athu onse anayenera kuperekedwa pa Iye, tiyenera kukhulupilira mu ubatizowo kuti mitima yathu iyeretsedwe ku uchimo kotheratu. 
Tiyeneranso kukhulupilira kuti mwazi wa Yesu unali chiweruzo cha machimo athu onse. Motero, onse amene akhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda ndi opulumutsidwa ku uchimo. 
Tiyenera kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu kuti tikalowe mu Ufumu wa Kumwamba. Iyi ndiyo njira yokhayo imene tingaomboledwere ku uchimo ndi kuthawa chiweruzo chachilungamo. 
Ubatizo wa Yesu mu Chipangano Chatsopano ndi kuika manja mu Chipangano Chakale ndi makalilole pa aliyense. Iwo ndi ogwirizana ndiponso omangana pakati pa Chipangano Chakale ndi Chipangano Chatsopano. 
Mu Chipangano Chatsopano, Yohane Mbatizi anabwera miyezi isanu ndi umodzi Yesu asanabwere. Pamene Yesu anabatizidwa, kunali, “Ciyambi cace ca     Uthenga Wabwino wa Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu” (Marko 1:1). Uthenga wabwino unayamba pamene Yesu anachotsa machimo a dziko kudzera mu ubatizo Wake. 
Utumiki wa chipulumutso wa mtundu wa anthu unali kuchitika kudzera mu mzere wa zochitika: Kubawa kwa Yesu, ubatizo Wake, kufa Kwake pa Mtanda, Kuukanso Kwake, ndiponso kukwera Kwake kwa Kumwamba. Pamene tikudziwa ndi kuzindikira mu njira ya chipulumutso mu mzere wa zochitika umenewu, ndife opulumutsidwa ku machimo athu onse. Ubatizo wa Yesu unali chiyambi cha uthenga wabwino pamene mwazi pa Mtanda unali chimaliziro Chake. 
“Ciyambi cace ca     Uthenga Wabwino wa Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu” (Marko 1:1). Sitingachotse china chilichonse cha ntchito yake ya chilungamo ―Ubatizo Wake, mwazi Wake pa Mtanda, kuuka Kwake, kukwera Kwake, kubweranso Kwake kwachiwiri―kuchokera ku uthenga wabwino wa Mwana wa Mulungu. 
Yesu anabwera kudzikoli mu thupi ndi kutsuka machimo onse a mtundu wa anthu ndi ubatizo Wake. Ichi chinali chiyambi cha uthenga wabwino wa kumwamba. Zikanakhala kuti chimodzi cha chimenezi chinasowa, uthenga wabwino wa kumwamba sukanakhala wanthunthu. 
Motero, ngati wina afuna kubadwanso mwatsopano, ayenera kukhulupilira mu ubatizo wa Kristu ndi mwazi Wake. Masiku ano, anthu ambiri sakukhulupilira choonadi cha ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Akuganiza kuti ubatizo wa Yesu ndi wamwambo chabe. Ichi ndi chinthu cholakwika kwambiri. Aliyense amene akhulupilira mwa Yesu ayeneranso kukhulupilira mu ubatizo Wake ndi mwazi. 
Kodi machimo athu angatsukidwe bwanji mwa kupempherera chikhululukiro kokha? Machimo athu onse anaperekedwa kwa Yesu pamene anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Panalibe njira ina kwa Iye imene akanachotsera machimo a mtundu wa anthu. 
Tiyenera kubadwanso mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu kuti tilowe mu Ufumu wa Kumwamba. Sikukanakhala chiombolo popanda madzi a ubatizo, mwazi wa pa Mtanda, ndi Mzimu. Yekhayo munthu amene anabadwa mwatsopano ndi amene angaone Mulungu, monga Yesu ananena kwa Nikodemo mu Yohane 3:5. Chipulumuso cheni cheni chimabwera pamene takhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. 
 
 

KODI TINGAPULUMUTSIDWE POPANDA UBATIZO WA YESU?


Kodi Yesu anakhala bwanji Mpulumutsi wathu?
Mwa kunyamula machimo athu onse kudzera mu ubatizo Wake

Kukanakhala kuti tinachotsako utumiki wa Ambuye wapoyera choona chakuti Yesu anabwera padzikoli ndi kuchotsa machimo athu onse kudzera mu ubatizo Wake, kapena kusayang’ana chiyero cha Yesu, amene anabadwa kwa Namwali Maria, kapena kunyalanyaza kukhulupilira mu Mtanda wa Yesu, Chikristu chikanakhala chipembezo chosaganiza bwino chimene chikutsogolera anthu kumafuula kuti “ndikhululukireni ine, ndikhululukireni ine” monga m’mene achibuda amachitira m’mipingo yawo. 
Kuchotsa ubatizo wa Yesu kungatanthauze kuti machimo athu sanaperekedwe pa Iye. Chikhulupiliro chathu chikanakhala chopanda ntchito, kutipanga ife kukhala osasiyana ndi wangongole amene akunena kuti analipira kale ngongole yake yonse koma choona n’chakuti sanalipire iliyonse. Kukanatipanga ife tonse kukhala abodza. Ngati wangongole akunena kuti analipira kale ngongole yake koma pamene sanalipire chilichonse, adzakhalabe ndi ngongole, zoona zake, ngakhalenso mu chikumbumtima chake. 
Yesu anatsuka okhulupilira kukhala oyera ndi madzi a ubatizo Wake ndikuwapanga iwo kukhala ana a Mulungu. Yesu anachotsa machimo onse a dziko kudzera mwa Yohane Mbatizi, kotero kuti okhulupilira onse ayeretsedwe. Pamene tadziwa ndi kukhulupilira chimenechi, mitima yathu imakhala yoyera kwamuyaya. 
Tiyamika Mulungu chifukwa cha chisomo Chake. Luka 2:14 anena kuti, “Ulemerero ukhale kwa Mulungu kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nao!” Chikhulupiliro chathu m’madzi ndi mwazi wa Yesu chitibweretsa ku chipulumutso chanthunthu ndi kutipanga ife kukhala ana a Mulungu. Ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake anapulumutsa ife ndi iye amene akhulupilira mu zinthu ziwiri izi ndiopulumuka. 
Palibe chimene tingachotsepo mu ntchito Zake. Ena amakhulupilira m’mwazi okha, akunena kuti mtumwi Paulo sanazitukumule chabe koma ndi Mtanda. Koma ubatizo wa Yesu unaphatikizidwanso ku Mtanda Wake. 
Tingathe kuona mu Aroma 6 kuti Paulo anabatizidwa mwa Kristu ndi kufa limodzi ndi Kristu. Ndiponso mu Agalatiya 2:20, “Ndinapacikidwa ndi Kristu; koma ndiri ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Kristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndiri nao tsopano m’thupi, ndiri nao m’cikhulupiriro ca Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha cifukwa ca ine .”
Ndipo mu agalatiya 3:27-29, “Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Kristu mudabvala Kristu. Muno mulibe Myuda, kapena Mhelene, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Kristu Yesu. Koma ngati muli a Kristu, muli mbeu ya Abrahamu, nyumba monga mwa lonjezano.” 
Kubatizidwa mwa Kristu kukutanthauza kukhulupilira mu zinthu zonse zimene anachita m’dziko lino, ubatizo Wake ndi mwazi Wake pa Mtanda. Kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake ndi kukhulupilira mu choonadi chakuti Yesu anachotsa kale machimo athu onse pafupifupi zaka zikwi ziwiri |(2000) zapitazo. Palibenso njira ina imene itibweretsa ife ku chipulumutso. 
 

TIMAPULUMUTSIDWA NDI MULUNGU PAMENE TAKHULUPILIRA MU UBATIZO WA YESU NDI MWAZI WAKE PA MTANDA 
 
Kodi machimo athu angatsukidwe pongopempha chikhululukiro?
Ai. Chikhululukiro cha uchimo chimatheka kudzera kokha mu chikhulupiliro chathu kuti machimo onse anaperekedwa kwa Yesu pamene anabatizidwa  ndi Yohane Mbatizi. 

“Pakuti ndi mtima munthu akhulupira kutengapo cilungamo; ndi m’kamwa abvomereza kutengapo cipulumutso” (Aroma 10:10).
“Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Kristu mudabvala Kristu” (Agalatiya 3:27). Chikhulupiliro chathu chimatitsogolera kuti tibatizidwe mwa Kristu, kuti tivale Khristu, ndiponso kuti tikhale ana a Mulungu. Pamene Yesu anabwera kudzikoli ndi kubatizidwa, machimo athu onse ndi machimo a dziko anaperekedwa kwa Iye. 
Chikhulupiliro chathu chatipangitsa ife kukhala m’modzi ndi Kristu. Tinafa pamene Iye anafa. Tinaukitsidwa pamene Iye anaukitsidwa. Tsopano chifukwa chakuti tinakhulupilira mu ubatizo wa Yesu, mwazi Wake, ndiponso kuuka Kwake, kukwera Kwake, tingalowe mu Ufumu wa Kumwamba ndi kukhala kwamuyaya. 
Pamene anthu akukhulupilira m’mwazi wa Yesu okha, sangathe koma kuzunzika ku uchimo umene unatsalira m’mitima yawo. Chifukwa chiani? Chifukwa chakuti sanadziwe kapena kuvomereza tanthauzo la ubatizo wa Yesu, umene unachotsa machimo awo onse ndi kuyeretsa mitima yawo yochimwa, kuwapanga kukhala oyera ngati matalala kwa muyaya. 
Kodi mumakhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake amene anapulumutsa inu ku machimo anu onse? Chonde khulupilirani mu choonadi chosasinthikachi. Popanda kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu, chikhulupiliro chanu chili chabe. Popanda kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu, simungaomboledwe ku machimo anu; mungapezeke mu chikondi chosayankhidwa. 
Iwo amene amakhulupilira mu Mtanda okha akunena kuti, “Yesu ndi Ambuye wanga, Mpulumutsi wanga, amene anafa pa Mtanda chifukwa cha ine. Iye anaukanso kwa akufa ndi kuchitira umboni ku chiukitso chake kwa masiku 40 asanakwere Kumwamba ndipo tsopano akhala kuzanja lamanja la Mulungu. Ndikhulupilira kuti adzabweranso kachiwiri kuzaweruza ife ndipo ndikupemphera kuti Yesu azandisintha kwanthunthu kuti ndikakumane naye. Oho, okondedwa wanga Yesu, Mbuye wanga.”
Amapempha chikhululukiro cha machimo awo ndipo amakhala ndi chiyembekezo chakuti alibe uchimo, koma muli uchimo mu mitima yawo. “Ndikhulupilira mwa Yesu koma ndili ndi uchimo mu mtima wanga. Ndimakonda Yesu koma ndili ndi uchimo mu mtima mwanga. Sindinganene kuti, “Chonde bwerani kwa ine, mkwati wanga’ chifukwa ndili ndi uchimo ndipo ndili ndi chikaiko pa chipulumutso changa, Choncho ndikhulupilira kuti Yesu adzabwera pamene ndili okonzeka bwino ndiponso pambuyo pakuti ndapemphera zolimba ndi kulapa molimba. Ndimakonda Yesu ndi mtima wanga onse koma sindingathe kukumana naye chifukwa cha machimo ali mu mtima mwanga.” 
Ngati Yesu angafunse anthu otere, “Kodi n’chifukwa chiani mukuganiza kuti ndinu operewera?” 
Iwo angayankhe kuti, “Ambuye, ndikudziwa kuti sindine olungama chifukwa ndimachimwa masiku onse. Choncho chonde ndiitaneni pamene mukuitana ochimwa.” 
Iwo sakudziwa kuti Mulungu, Mlengi ndiponso Oweruza, sadzalola ochimwa kapena kuwapanga iwo kukhala ana Ake. 
Mkwati anabwera ndi kukonza mavuto onse a uchimo a mkwatibwi, koma chifukwa mkwati sanadziwe choona chimenechi, iye anazunzidwa. Pamene tikuganiza kuti ndife ochimwa chifukwa tachimwa ndi thupi lathu, tilibe chikhulupiliro mwa Mulungu, Pamene sitikudziwa kapena kuzindikira choonadi cha mawu a Mulungu, machimo mu mitima yathu akupitiliza kuchuluka. 

Kodi n’chifukwa chiani anthu ena Amavutika ndi uchimo m’mitima yawo?
Chifukwa sanadziwe kapena kuvomereza m’mitima yawo tanthauzo la ubatizo wa Yesu umene unachotsa machimo awo onse.

Mkwati anachotsa machimo a dziko. Kuti? Pa Yordano pamene Iye anabatizidwa. Iwo amene sakhulupilira zimenechi adakali ochimwa. Akhalabe mkwatibwi ochimwa. 
Mkwati akufunsa mkwatibwi, “Kodi ungandikonde bwanji pamene sindiwe mkwatibwi Wanga? Usanandiitane Ine mkwatiwako, machimo ako onse ayenera kutsukidwa.” 
Kodi tingaomboledwe popanda ubatizo wa Yesu? Ai! Tinalengedwa m’chifanizo cha Mulungu, choncho timapempa chilungamo mu mitima yathu, ndipo chikumbumtima chathu chimayesa kukhala cholungama, nachonso. Koma ndi kosatheka kwa ife kuganiza kuti ndife opanda chimo ngati mitima yathu sinayeretsedwa. Pokhapo ngati tavomereza ndi kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi pamene tinganenedi kuti tilibe uchimo ndipo ndife olungama.
Chikumbumtima chathu sichingakhale choyeretsedwa ngati tiziona tokha kuti tilibe uchimo zoona zake tili ndi uchimo m’mitima yathu. Kapena Mulungu kutivomera pansi pa zochitika zimenezi. Mulungu sanama. 
Mulungu anauza Mose kuti awerenge anthu a mu Israyeli kuti alipire malipiro a miyoyo yawo. Olemera sankayenera kupereka kupitilira theka ndiponso osauka sankafunika kupereka zochepa. Aliyense ankafunika kulipira chikole. 
Motero, kodi munthu angakhale oyeretsedwa ngati sakhulupilira mwa Yesu amene analipirira iye malipiro a moyo wake? Munthu otere akupitilizabe kukhala ndi uchimo mu mtima mwake. 
Pamene tikhulupilira mu mwazi okha wa Yesu, tili ndi uchimo mu mitima yathu ndipo tiyenera kuulula kuti ndife ochimwa. Koma ngati tikhulupilira mu uthenga wabwino wa ubatizo Wake ndi Mtanda pamodzi, tinganene moona kuti tilibe uchimo. Chipulumutso ndi moyo osatha ndi zathu. 
 
 

KUNYOZERA MZIMU 


Kodi ndi uchimo otani umene uweruzira munthu ku gehena?
Kuchimwira Mzimu, Mwanjira ina, osakhulupilira mu ubatizo wa Yesu

Aroma 1:17 anena kuti, “Pakuti m’menemo caonetsedwa cilungamo ca Mulungu cakucokera kucikhulupiriro kuloza kucikhulupiriro.” Chilungamo cha Mulungu chinavumbulutsidwa mu uthenga wabwino. Yesu Kristu anabwera kudzikoli ndi kutsuka machmo athu onse ndi ubatizo Wake ndiponso imfa Yake pa Mtanda. Ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake ndi mphamvu ya uthenga wabwino. Yesu anatsuka machimo athu kamodzi kokha. 
Kukhulupilira kukutanthauza chipulumutso ndipo kusakhulupilira kukutanthauza gehena osatha. Atate wathu wa Kumwamba anatuma Mwana Wake obadwa yekha Yesu kudzikoli ndipo anamlola kubatizidwa kuti atetezere machimo athu. Motero, iye amene akhulupilira mwa Iye angayeretsedwe ku zolakwa zake zonse. 
Tchimo lokha limene linatsala m’dzikoli ndi uchimo wa kusakhulupilira mu ubatizo Wake ndi mwazi. Kusakhulupilira ndi kunyozera Mzimu ndiponso uchimo umene uzaweruzidwa ndi Mulungu, Kuweruza osakhulupilira ku gehena. Ndi uchimo waukulu pa onse. Aliyense wa inu amene achita tchimo limeneli ayenera kulapa ndi kuomboledwa mwa kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu. Ngati simutero, muzaonongedwa kwa muyaya. 
Kodi munapulumutsidwa ndi umboni wa chiombolo kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi? Kodi munalandira umboni wa Yohane monga analembera mu Yohane 1:29, “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” Kodi mumakhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake monga analembera mu Ahebri 10:18, “Koma pomwe pali cikhululukiro ca macimo palibenso copereka ca kwa ucimo.” 
Mulungu amachonga iwo amene akhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake m’mitima yawo. Mulungu amawapanga iwo kukhala ana Ake. Iwo amene akhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake ali oomboledwa kudzera mu chilungamo cha chikondi cha Yesu. 
Aliyense amene Mulungu watuma amayankhula za mawu a Mulungu, koma iwo amene ali a dziko lapansi, amene sanatumidwe ndi Mulungu, amalalikira mogwirizana ndi maganizo awo. Pali ambiri padzikoli amene akulalikira mawu a Mulungu, komanso iwo amene anatumidwa ndi Mulungu amayankhula za ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. 
Koma iwo amene akulalikira mawu awo amangozionetsera maganizo awo. Iwo amanena kuti, “Ndife owomboledwa ku tchimo loyamba lokha, koma aliyense ayenera kulapa machimo ake masiku onse.” Iwo amanena kuti ayenera kuyeretsedwa pang’onopang’ono. 
Koma kodi munthu angaziyeretse pa iye yekha? Kodi tingaziyeretse tokha pa mphamvu za kuchita bwino kwathu ndiponso pa kuyesayesa kwathu? Kodi timayeretsedwa chifukwa chakuti Mulungu anatsuka machimo athu onse, kapena chifukwa chakuti timayesa kupeza chiombolo pa ife tokha? 
Chikhulupiliro choona ndi chimene chimayeretsa ife. Kodi tingapange makala kukhala oyera mwa kuwatsuka ka nthawi zambiri? Kodi tingapange thupi lakuda kukhala loyera poikako soda? Palibe sopo ochuluka bwanji kapena soda angatsuke machimo athu, ndiponso chilungamo chathu chili ngati zonyansa za padzala. Kodi timakhala olungama mwa kukhulupilira ubatizo wa Yesu ndi mwazi kapena mu mwazi okha wa pa Mtanda? 
Chikhulupiliro choona chichokera ku madzi a ubatizo wa Yesu ndi mwazi pa Mtanda. Chipulumutso sichibwera chifukwa cha kuyesayesa kwanu. Chikhulupiliro chathu chokha mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake ndi chimene chitimasula ku uchimo ndi kutipanga kukhala olungama. 
Atate anapereka anthu onse m’manja mwa Mwana Wake, ndipo onse amene akhulupilira mwa Iye adzakhala ndi moyo osatha. Kukhulupilira mwa Mwana kukutanthauza kukhulupilira mu chiombolo kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi. Iwo amene akhulupilira adzakhala ndi moyo osatha ngati mwana wa Mulungu. Iwo amene anapulumutsidwa anakhala ku zanja lamanja la Mulungu kwamuyaya. 
Chikhulupiliro mu ubatizo wa Yesu ndi umodzi Wake ndi Mulungu ndi chikhulupilironso mu Mzimu. Mawu a choonadi amatilola kubadwa mwatsopano. Timapulumutsidwa mwa kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. 
Khalani ndi chikhulupiliro. Kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake ndi kupeza chiombolo. Khalani ndi chikhulupiliro mu choonadi cha uthenga wabwino ndipo pezani chikhululukiro cha uchimo.