• All e-books and audiobooks on The New Life Mission website are free
  • Explore multilingual sermons in global languages
  • Two new revised editions in English have been released
  • Check out our website translated into 27 languages
Search

Sermons

Mutu 3: Uthenga Wabwino wa Madzi ndi Mzimu Woyera

[3-9] Tiyeni Tichite Chifuniro cha Atate ndi Chikhulupiriro (Mateyu 7:21-23)

Tiyeni Tichite Chifuniro cha Atate ndi Chikhulupiriro(Mateyu 7:21-23)
“Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakucita cifuniro ca Atate wanga wa Kumwamba. Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mau m’dzina lanu, ndi m’dzina lanunso kuturutsa mizimu yoipa, ndi kucita m’dzina lanunso zamphamvu zambiri? Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, sindinakudziwani inu nthawi zonse; cokani kwa Ine, inu akucita kusayeruzika.”
 

MWINA NDINE AMENE… 

Kodi aliyense amene akunena kuti Ambuye, Ambuye adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba?
Ai. Okhao ochita chifuniro cha Mulungu

Yesu Kristu ananena kuti, “Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakucita cifuniro ca Atate wanga wa Kumwamba.” Mawu amenewa abweretsa mantha mu mitima ya Akristu ambiri, kuwapangitsa kugwira ntchito molimbika kuti achite chifuniro cha Mulungu. 
Akristu ambiri amaganiza kuti chinthu chokha chimene ayenera kuchita ndi kukhulupilira mwa Yesu kuti alowe mu Ufmu wa Kumwamba, Koma Mateyu 7:21 akutiuza kuti osati onsa amene akunena kwa Iye, ‘Ambuye, Ambuye adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba. 
Ambiri amene akuwerenga ndime imeneyi akudankhawa “Mwina ndine amene.” Amayesa kudzilimbitsa, “Ai, Yesu ayenera anatanthauza osakhulupirira.” Komabe maganizo amakhalilira m’maganizo mwawo ndipo akupitiliza kuwavutitsa. 
Choncho, amakakamira pa ndime imene ikunena kuti, “koma wakucita cifuniro ca Atate wanga wa Kumwamba.” Iwo amakakamira ku mawu akuti, ‘wakuchita cifuniro ca Atate” ndipo amaganiza kuti angachite zimenezo mwa kupereka chakhumi mokhulipirika, kupemphera m’banda kucha, kulalikira, kuchita zinthu zabwino, ndi kusachimwa…ndi zina zotereo. Amayesa mwamphamvu. Zimandimvetsa chisoni ndikaona iwo. 
Anthu ambiri amalakwitsa chifukwa samvetsetsa ndime imeneyi. Motero ndikufuna kufotokoza ndime imenei momveka bwino kuti ife tonse tidziwe chifuniro cha Mulungu ndi kukhala mwa icho. 
Choyamba, tiyenera kudziwa kuti chifuniro cha Mulungu ndi chakuti Mwana Wake achotse machimo a anthu onse ndipo motero amasule ife ku uchimo. 
Mu Aefeso 1:5, munalembedwa kuti, “Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana a Iye yekha mwa Yesu Kristu, monga umo kunakomera cifuniro cace.” 
Mwanjira ina, cholinga Chake ndi chakuti ife tidziwe uthenga wabwino oonadi umene Yesu Kristu anatsukira machimo athu onse, motero kutilola ife kuti tibadwe mwatsopano. Iye akufuna kuti ife tibadwe mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu popereka machimo athu onse pa Mwana Wake, Yesu. Ichi ndi chifuniro cha Mulungu.
 

KUNENA KOKHA KUTI, “AMBUYE! AMBUYE!” 

Kodi tiyenera kudziwa chiani pamene tikhulupilira mwa Yesu?
Chifuniro cha Atate

“Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakucita cifuniro ca Atate wanga wa Kumwamba.” (Mateyu 7:21). 
Tiyenera kuzindikira chifuniro cha Atate m’njira ziwiri. Choyamba, tiyenera kudziwa kuti ndi chifuniro Chake kuti tipeze chikhululukiro cha machimo athu ndi kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Chachiwiri, tiyenera kugwira ntchito mochokera ku chikhulupiliro chimenecho. 
Ndi chifuniro Chake kuchotsa machimo a anthu onse padziko lapansi. Satana anabweretsa kugwa kwa makolo athu Adamu kudzera mu uchimo. Koma chifuniro cha Atate wathu ndi kuchotsa machimo onse a munthu. Tiyenera kudzindikira kuti sichifuno cha atate wathu kuti ife tizipereka chakhumi mwachikhulupiliro ndi kupemphera m’banda kucha, koma kutipulumutsa ku uchimo onse. Ndi chifuniro Chake kupulumutsa ife tonse ku kumira mu Nyanja yauchimo. 
Baibulo limanena kuti si aliyense amene akunena kuti ‘Ambuye, Ambuye’ adzalowa mu ufumu wa Kumwamba. Ichi chikutanthauza kuti sitiyenera kukhulupilira kokha mwa Yesu, koma kudziwanso chimene Atate wathu akufuna kwa ife. Ndi chifuniro Chake kutipulumutsa ife ku uchimo ndi chiweruzo cha ku gehena, podziwa kuti cholowa cha Adamu ndi Hava chikutanthauza kuti sitingathandize koma kukhala mu uchimo. 
 
 

CHIFUNIRO CHA ATATE 


Kodi chifuniro cha Mulungu ndi chiani?
Kutipanga ife kukhala ana Ake mwa kutimasula ku uchimo

Mateyu 3:15 akunena kuti, “Pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero” Motero kunali kukwaniritsa chikonzero cha Mulungu kuti Yesu anabwera kudzikoli kuzapulumutsa ife ku uchimo. Chifuniro cha Mulungu chinakwaniritsidwa pamene Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. 
Iye anafuna kutipulumutsa ndi kutipanga kukhala ana Ake. Kuti achite zimenezo, Mwana Wake anayenera kuchotsa machimo athu onse. Ndi chifuniro Chake kupanga anthu onse kukhala ana Ake. Choncho anatuma Mwana Wake kuti achotse machimo a anthu onse amene anagwera mumsampha wa Satana. Ndi chifuniro Chake kupereka moyo wa Mwana Wake chifukwa cha anthu onse kotero kuti akhale ana Ake. 
Pamene Yesu anabatizidwa ndi kufa pa Mtanda, chifuniro cha Mulungu chinakwaniritsidwa. Ndi chifunironso Chake kuti ife tikhulupilire kuti machimo athu onse anaperekedwa pa Yesu pamene anabatizidwa ndiponso kuti ananyamula chiweruzo cha zolakwa zathu zonse kudzera mu imfa Yake ya pa Mtanda. 
“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wace wobadwa yekha” (John 3:16). Mulungu anapulumutsa anthu Ake ku uchimo. Kuti achite zimenezo, chinthu choyamba chimene Yesu anachita mu utumiki Wake wa pagulu ndi kubatizidwa ndi Yohane Mbatizi. 
“Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, “Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero. Pamenepo anamlola Iye” (Mateyu 3:15). Ndi chifuniro cha Mulungu kuti Yesu abwere kudzikoli, kuzachotsa machimo onse a dziko kudzera mu ubatizo Wake, kufa pa Mtanda ndi kuukitsidwa. 
Tiyenera kudziwa zimenechi bwinobwino. Anthu ambiri amawerenga Mateyu 7:21 ndi kuganiza kuti ndi chifuniro Chake kuti ife titumikire Ambuye, ngakhale mpaka kufa, mwa kupereka katundu wathu yense wa dziko kuti timangire mipingo. 
Akristu anzanga, ife amene tikhulupilira mwa Yesu tiyenera choyamba kudziwa chifuniro cha Mulungu ndi kuchichita. Ndi kulakwa kuti inu mudzipereke nokha ku mpingo popanda kudziwa chifuniro Chake. 
Anthu amadzifunsa okha n’chiani china chingakhaleko kuchotserapo kukhala m’chikhulupiliro mkati mwa mipingo yawo ya chikhulupiliro choona. Koma ine ndekha ndinaphunzira chiphunzitso cha kavini ku Mpingo wa Presbyterian ndipo ndinakula ndi amai opeza amene anali achipembezo monga mbusa wina aliyense wakale. Ndinaphunzira mu mpingo umenewu otchedwa kuti chikhulupiliro choona. 
Mtumwi Paulo nayenso anati angazitame kuti anali ochokera ku fuko la Benjamini ndipo anaphunzira Lamulo kwa Gamaliyeli, amene anali mpunzitsi wamkuru panthawi imeneyo. Paulo asanabadwe mwatsopano, anali kupita kukamanga iwo amene anali kukhulupilira mwa Yesu. Koma anapeza chikhulupiliro mwa Yesu pa njira ya ku Damasiko ndipo anakhala olungama kudzera mu dalitso la kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. 
 
 

TIYENERA KUDZIWA CHIFUNIRO CHA MULUNGU TISANACHICHITE 


Kodi chofunika ndi chiani tisanakhulupilire mwa Yesu?
Tiyenera poyamba kudziwa chifuniro Chake.

Chiyeretso chathu ndi chifuniro cha Mulungu. “Pakuti ici ndi cifuniro ca Mulungu, ciyeretso canu, kuti mudzipatule kudama” (1 Atesalonika 4:3). Tikudziwa kuti ndi chifuniro cha Mulungu kuti tikhale oyera kudzera m’madzi ndi Mzimu ndi kukhala m’chikhulupiliro pa miyoyo yathu yonse. 
Ngati pali wina aliyense amene akhulupilira mwa Yesu koma adakali ndi uchimo mu mtima mwake, sakukhala mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Kutsatira chikhulupiliro Chake kukufuna kuyeretsedwa kudzera mu chipulumutso chopezeka mwa Yesu. Kudziwa zimenezi ndi kuchita chifuniro cha Mulungu. 
Pamene ndikufunsani, “Kodi mudakali ndi uchimo mu mtima mwanu ngakhale kuti mumakhulupirira mwa Yesu?” ndipo yankho lanu ndilakuti inde, ndiyeno simukudziwa bwino chifuniro cha Mulungu. Ndi chifuniro cha Mulungu kuti tiyenera kuyeretsedwa ndi kupulumutsidwa ku machimo onse kudzera mu chikhulupiliro cha mu madzi ndi Mzimu. 
Kale kunali munthu amene anali ndi ana omvera. Tsiku lina anaitana wamkulu, amene analinso omvera kwambiri, ndi kunena kuti, “Mwana wanga, pita ku mudzi odutsa munda…” 
Asanamalize kuyankhula, mwana uja anati “Inde atate” ndipo ananyamuka. Sanayembekeze kufufuza kuti ayenera kukachita chiani. Anangonyamuka. 
Atate ake anamuitana, “Mwana wanga, n’kwabwino kuti ndiwe omvera koma uyenera kudziwa chimene ndikufuna kuti ukachite.” 
Koma mwanayo anati, “zilibwino zonse, atate. Ndidzakumverani. Ndani angamvere koposa ine?” 
Koma indedi anabwerako opanda kanthu. Analibe njira iliyonse yochitira chifuniro cha atate ake popanda kudziwa chimene anali kufuna. Anangomvera mwakhungu. 
Tingakhale monga iye ngati sitikudziwa Yesu Kristu. Ambiri amadzipereka okha, kutsatira ziphunzitso zaumulungu, kupereka chakhumi mwachikhulupiriro, kupemphera usiku onse ndi kusala chakudya, zonse posadziwa chifuniro cha Mulungu. 
Pamene afa ndi uchimo m’mitima yawo, amawabweza pa chipata cha Kumwamba. Ali ofunitsitsa kuchita chifuniro cha Mulungu koma sanadziwe chimene Mulungu ankafuna. 

Kodi zikutanthauzanji Kuchita kusayeruzika?
Kukhulupilira mwa Yesu uli ochimwa pamene sukudziwa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu

“Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mau m’dzina lanu, ndi m’dzina lanunso kuturutsa mizimu yoipa, ndi kucita m’dzina lanunso zamphamvu zambiri? Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, sindinakudziwani inu nthawi zonse; cokani kwa Ine, inu akucita kusayeruzika!” (Mateyu 7:22-23)
Pali zinthu zimene Mulungu akufuna kuti ife tichite, ndipo pali chikhulupiliro chimene Iye akufuna kwa ife. Iye akufuna ife tikhulupilire kuti Yesu anachotsa machimo athu onse. Ambiri amanenera, akuchotsa ziwanda, ndipo akuchita zodabwitsa m’dzina Lake popanda kudziwa choonadi cha madzi ndi Mzimu. 
Kuchita zodabwitsa kukutanthauza kumanga mipingo yambiri, kugulitsa katundu wake kuti asonkhe ku mpingo, kupereka moyo wake chifukwa cha Ambuye, mwa zinthu zina. 
Kunenera m’dzina lake kukutanthauza kukhala mtsogoleri. Anthu otere ali ngati Afalisi amene ankazitukumula za kakhalidwe kulingana ndi Lamulo kwinaku akukalipitsa Yesu. Izinso zikusonyeza ku amene adzakhala-Akristu a chikhulupiliro choona. 
Kuchotsa ziwanda ndi kuchita mphamvu. Onse ali odalilika pa chikhulupiliro chawo, koma Ambuye adzawauza pothera kuti sakuwadziwa. Iye adzawafunsa kuti angam’dziwe Iye bwanji pamene Iye sakuwadziwa. 
Ambuye akuti, “Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, sindinakudziwani inu nthawi zonse; cokani kwa Ine, inu akucita kusayeruzika!” Pa tsiku limenelo, chikhamu cha anthu chidzafuula kwa Iye, “Ambuye, ndikhulupilira. Ndikhulupilira kuti ndinu Mpulumutsi wanga.” Adzanena kuti amamukonda koma ali ndi uchimo m’mitima yawo.” Ambuye adzawaitana kuti anthu akuchita kusayeruzika (ochimwa amene amene sanaomboledwe) ndipo adzawauza kuti achoke kwa Iye. 
Pa tsiku limenelo, iwo amene anafa popanda kubadwa mwatsopano adzalira pamaso pa Yesu. “Ndinanenera, kumanga mipingo ndi kupereka atumiki oyendayenda 50 kunja m’dzina Lanu.” 
Koma Yesu adzanena kwa ochimwawo, “cokani kwa Ine, inu akucita kusayeruzika!” 
“Kodi mukutanthauza chiani? Kodi simudziwa kuti ndinali kunenera m’dzina Lanu? Ndinatumikira mu mpingo kwa zaka zambiri…ndinaphunzitsa ena kuti akhulupilire mwa Inu. Kodi bwanji simukundidziwa ine?” 
Iye azayankha, “sindikudziwani. Inu amene mukunena kuti mukundidziwa Ine koma muli ndi uchimo mu mtima mwanu, chokani kwa Ine!” 
Ndi kusayeruzika pamaso pa Mulungu kukhulupilira mwa Iye ndi uchimo mu mtima kapena kusakhulupilira mogwirizana ndi lamulo Lake la chipulumutso. Ndi kusayeruzika kusadziwa chifuniro Chake. Ndi kusayeruzika kuchita chifuniro Chake popanda kuchidziwa kapena kusadziwa dalitso la kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Ndiponso ndi kusayeruzika kusamvera chifuniro Chake. Kusayeruzika ndi tchimo.
 
 

CHIFUNIRO CHA MULUNGU MU BAIBULO 


Kodi ana a Mulungu Ndi ndani?
Olungama amene alibe tchimo

Ndi chifuniro Chake kuti ife tikhulupilire mu uthenga wabwino wa kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Uthenga wabwino oona umalimbikitsa kubadwanso kwathu. Ndiponso ndi chifuniro Chake kuti tikhale mu uthenga wabwino ngati ana Ake. Tiyenera kudziwa chifuniro cha Mulungu, koma ambiri sadziwa uthenga wabwino wa kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. 
Pamene ndafunsa anthu chifukwa chimene akukhulupilira mwa Yesu, ambiri amanena kuti akukhulupilira mwa Yesu pofuna kuti akhululukidwe ku machimo awo. 
Ndafunsa, “Ndiyeno, kodi muli ndi uchimo mu mtima mwanu?” 
Iwo amati, “Indedi, ndili nawo.” 
“Ndiyeno, kodi ndinu opulumutsidwa kapena ai?” 
“Indedi ndine opulmutsidwa.”
“Kodi ochimwa amene ali ndi uchimo mu mtima mwake angalowe mu ufumu wa Kumwamba?”
“Ai, iye sangalowe.” 
“Ndiyeno, kodi mukupita ku ufumu wa Kumwamba kapena ku moto wa ku gehena?” 
Iwo amanena kuti akupita ku ufumu wa Kumwamba, koma kodi angatero? Iwo adzapita ku gehena. 
Ena amaganiza kuti chifukwa chakuti akukhulupilira mwa Yesu, angalowe mu ufumu wa Kumwamba ngakhale kuti ali ndi uchimo m’mitima yawo ndipo kuti ndi chifuniro cha Mulungu kuti iwo akhale choncho. Koma Mulungu samalola ochimwa ku ufumu wa Kumwamba. 
Kodi chifuniro cha Mulungu ndi chiani? Kunanenedwa Mbaibulo kuti chifuniro cha Mulungu ndi chakuti kuti ife tikhulupilire mwa Mwana Wake, kuti tikhulupilire mu dalitso la kuomboledwa kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda. 
Iwo amene akhulupilira mu dalitso la kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu amakhala ana Ake. Ndi ulemerero wathu kukhala ana ake. Ana Ake ndi olungama. 
Pamene Mulungu akuitana ife olungama, kodi amaona Mkristu-ochimwa ngati olungama? Mulungu sanganame. Choncho pamaso pa Iye, muli ochimwa kapena munthu olungama. Pamenepo ‘sangaonedwe ngati opanda uchimo.’ Iye amaitana iwo okha amene akhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu kuti oyeretsedwa. 

Kodi tingakhale bwanji ana a Mulungu?
Mwa kuvomereza uthenga wabwino wa madzi ndi magazi

Chifukwa Mulungu anapereka machimo onse a dziko kwa Mwana Wake, ngakhale Mwana Wake anayenera kuweruzidwa pa Mtanda. Mulungu sanganame bodza. Iye anati, “Pakuti mphotho yace ya ucimo ndi imfa” (Aroma 6:23). Pamene Mwana Wake anafa, mdima unagwera pa dziko lapansi kwa maola atatu. 
“Ndipo poyandikira ora lacisanu ndi cinai, Yesu anapfuula ndi mau akuru, kunena, Eli, Eli, lama sabakitani? Ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?” (Mateyu 27:46)
Yesu anachotsa machimo onse a dziko kudzera mu ubatizo Wake kuti apulumutse anthu onse ku machimo awo. Iye anachotsa machimo a anthu onse, podziwa kuti anayenera kupachikidwa ndi kusiidwa ndi Mulungu, Atate Wake. Choncho Mulungu anaweruza Mwana Wake chifukwa cha machismo amene Iye ananyamula pa Yordano ndi kutembenuza nkhope Yake kwa Mwana Wake kwa maola atatu. 
“Koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lace.” (Yohane 1:12). 
Kodi ndinu ana a Mulungu? Ndife obadwa mwatsopano chifukwa tinavomereza uthenga wabwino wakubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Iwo amene ndi obadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu ndi olungama. Tsopano tonse takhala olungama. 
“Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?” (Aroma 8:31). Pamene munthu olungama akuziitana yekha kuti olungama pamaso pa Mulungu ndi anthu, iwo amene sanaomboledwe amayesa kumuweruza. Choncho mtumwi Paulo anati, “Ndani adzaneneza osankhidwa a Mulungu? Mulungu ndiye amene awayesa olungama” (Aroma 8:33). Mulungu anachotseratu machimo athu onse kudzera mwa Yesu ndi kutchula kuti oyeretsedwa, olungama, ndiponso ana Ake. Iye anatipatsa ufulu okhala ana aulemerero a Mulungu. 
Iwo amene anabadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu ndi ana Ake. Akukhala naye kwamuyaya. Iwo sialinso olengedwa wamba m’dzikoli koma ana a Mulungu amene akukhala Kumwamba. 
Tsopano popeza ndi ana olungama a Mulungu, palibe amene angawaimbe mlandu, kuwaweruza, kapena kuwapatula kwa Mulungu. 
Tiyenera kudziwa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu kuti tikhulupilire mwa Yesu. Tiyenera kudziwa Baibulo. Ndi kofunika kuti tidziwe ndi kukhulupilira chifuniro cha Mulungu pofuna kuti tithe kuchita bwino mogwirizana ndi chifuniro Chake. 
 
 

KODI NDI CHIFUNIRO CHA MULUNGU KUTI OCHIMWA ABADWE MWATSOPANO MWA MADZI NDI MZIMU 


Kodi chifukwa chiani Mulungu anatuma Mwana Wake m’chifaniziro cha munthu ochimwa?
 Kuti machimo onse aperekedwe kwa Iye
 
Ndi chifuniro cha Mulungu kuti tikhale owomboledwa ndi kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. “Pakuti ici ndi cifuniro ca Mulungu, ciyeretso canu” (1 Atesalonika 4:3). 
Chinali chifuniro cha Mulungu kuti atumize Mwana Wake kuti machimo onse aperekedwe kwa Iye ndi kuti ife tipulumutsidwe. Ili ndi lamulo la Mzimu limene likulola ife kuti tibadwe mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Chinatimasula ku machimo onse. 
Ndife owomboledwa. Tsopano kodi nonse mwazindikira chifuniro cha Mulungu? Ndi chifuniro Chake kuti aombole ife tonse. Sakufuna kut ife tisakanizane ndi dziko koma m’malo mwake tikhulupilire m’mawu Ake okha ndi kupembeza Iye Yekha. 
Ndi chifunironso cha Mulungu kuti iwo amene anabadwa mwatsopano achitire umboni uthenga wabwino ndi kukhala mu mpingo, kuzipereka okha ku ntchito yobweretsa miyoyo ina kwa Mulungu. 
Timachimwa osati chifukwa chakuti tikufuna, koma chifukwa ndife ofoka. Koma Yesu anachotsa machimo onse amenewo. Mulungu anapereka machimo onse a dziko kwa Yesu kudzera mwa Yohane Mbatizi. Iye anatuma Mwana Wake yekha pa chifukwa chimenecho ndi kumupangitsa kuti abatizidwe ndi Yohane. Ndife opulumutsidwa pokhulupilira mwa ichi. Ichi ndi chifuniro cha Mulungu. 
 

NDI CHIFUNIRO CHA MULUNGU KUTI IFE TIKHULUPILIRE MWA YESU, AMENE IYE ANATUMA 

Kodi chifukwa chiani Yesu anabwera m’chifaniziro cha munthu ochimwa?
Kuti achotse machimo onse a mtundu wa anthu

Baibulo limanena kuti kuchita chifuniro cha Mulungu ndi kukhulupilira mwa Iye amene anamtuma. “Pamenepo anati kwa Iye, Ticite ciani, kuti ticite nchito za Mulungu? Nchito ya Mulungu ndi iyi, kuti mukhulupirire Iye amene Iyeyo anatuma. Cifukwa cace anati kwa Iye, ndipo mucita cizindikilo canji, kuti tione ndi kukhulupirira Inu? Atate athu anadya mana m’cipululu; monga kwalembedwa, Mkate wocokera m’mwamba anawapatsa iwo kudya.” (Yohane 6:28-31). 
Anthu anauza Yesu kuti Mulungu anapatsa Mose chizindikiro pamene anali kupita ku Kanani, Kupatsa Israyeli mana ochokera Kumwamba, ndipo pa chifukwa ichi anakhulupilira mwa Mulungu (Yohane 6:32-39). Anthu anafunsa Yesu, “Ticite ciani, kuti ticite nchito za Mulungu?” 
Yesu anayankha kuti ayenera kukhulupilira mwa Iye kuti achite ntchito ya Mulungu. Ngati tingachite ntchito ya Mulungu, tiyenera kukhulupilira mu ntchito za Yesu Kristu. Ndi chifuniro cha Mulungu kuti ife tisakhulupilire ndi kulalikira kokha uthenga wabwino koma kukhalanso mwa iwo. 
Mulungu anatilamula, “Cifukwa cace mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu; ndipo onani, Ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira cimariziro ca nthawi ya pansi pano” (Mateyu 28:19-20).
Yesu anatiuza poyera kuti tibatizidwe m’dzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Oyera. Zonse zimene anachitira Atate Wake ndi Mzimu zinalowa mu ubatizo Wake. Pamene tikumvetsetsa chimenechi, tingakhulupilire mwa Mulungu ndi kuona zonse zimene Yesu anachita m’dzikoli ndi m’mene Mzimu unachitira umboni ku zimenezo. 
Yesu anatumizidwa ndi Mulungu kuti achitire umboni ku uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Motero pongokhulupilira m’mawu a Mulungu ndi mwa atumiki Ake ndi pamene tingapulumutsidwe. 
 
 

KUCHITA NTCHITO YA MULUNGU 


Kodi cholinga cha miyoyo yathu ndi chiani?
Kuchita chifuniro cha Mulungu mwa kufalitsa uthenga wabwino padziko lonse lapansi

Ngati tingachite ntchito ya Mulungu, choyamba tiyenera kukhulupilira mu uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi imfa Yake ya pa Mtanda. Ndi ntchito ya Mulungu kukhulupilira mwa Iye amene Mulungu anatuma. Kuti tikhulupilire mwa Yesu, tiyenera choyamba kukhulupilira kuti anatipulumutsa ndi madzi komanso mwazi. 
Chifuniro cha Mulungu chinamalizika mwa ife pamene tinakhulupilira mwa Yesu ndi kulalikira uthenga wabwino. Mwa njira imeneyi tikuchita ntchito ya Mulungu. Iye anatiuza kuti okhao amene akhulupilira mu dalitso la kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu ndi amene angalowe mu ufumu wa Kumwamba. 
Tiyeni tonse titenge malo athu a Kumwamba mwa kuzindkira zoonadi zofunkira izi. Kuzindikira chifuniro choona cha Mulungu, podziwa ndi kukhulupilira kuti machimo athu onse anaperekedwa kwa Yesu ndi ubatizo Wake. Khalani mwa kukulitsa ufumu Wake. Pomaliza, lalikirani uthenga wabwino kufikira tsiku limene mudzafe. 
Akristu anzanga! Iwo amene akhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndi amene akuchita ntchito ya Mulungu. Ndi ntchito ya Mulungu kukhulupilira mwa Iye amene anatuma. Ndi kuchita chifuniro Chake kukhulupilira kuti machimo onse anaperekedwa kwa Iye amene Mulungu anatuma ndiponso kuti Yesu Kristu ndi Mpulumutsi wathu. 
Ntchito ya kuombola munthu ku uchimo inamalizika pamene Yesu anabatizidwa pa Yordano ndi kutifera pa Mtanda. Ntchito yachiwiri ya Mulungu ndi kukhulupilira mwa Iye amene anatuma, kukhulupilira mwa Mpulumutsi amene anachota machimo a dziko, ndi kulalikira uthenga wabwino padziko lonse lapansi. 
Tsopano ife amene tinabadwa mwatsopano tiyenera kukhala ndi kulalikira uthenga wabwino kufikira kumalekezero a dziko. 
 
Kodi anthuwo amene akhulupilira mwa Yesu popanda kudziwa chifuniro cha Mulungu amapita kuti?
Amapita kugehena.

“Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mau m’dzina lanu, ndi m’dzina lanunso kuturutsa mizimu yoipa, ndi kucita m’dzina lanunso zamphamvu zambiri? Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, sindinakudziwani inu nthawi zonse; cokani kwa Ine, inu akucita kusayeruzika!” (Mateyu 7:22-23) 
Ndime imeneyi ikutiuza poyera amene ali ochimwa pamaso pa Mulungu ndiponso amene ali kuchita kusayeruzika. 
Kuli ambiri amene sanabadwe mwatsopano mwa iwo amene akunena kuti, ‘Ambuye, Ambuye.’ Iwo ali mu zowawa chifukwa adakali ndi uchimo mu mitima yawo. Choncho amalilira kwa Mulungu, Kuitana, ‘Ambuye, Ambuye,’ mu theka la chikhalidwe chosayenera, kusokoneza mapemphero oona a kupembeza. 
Akukhulupilira kuti chikumbumtima chawo chizayeretsedwa ngati angalilire m’mapemphero, koma ndi zosatheka chifukwa uchimo ukukhalabe mu mitima yawo. Iwo amapemphera mapiri, kulira movutikira, ngati kuti Mulungu anali kutali kwambiri. Pamene tilibe chikhulupiliro chonse, timayamba kuitana ‘Ambuye, Ambuye’ pafupipafupi mopitiliza. 
Mu mipingo ina m’mene osonkhana awo sanabadwe mwatsopano, amapemphera ndi chifuniro chonse kotero kuti guwa limaphwanyika. 
Koma tingaone mu Baibulo kuti si onse amene akuitana kuti ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa mu ufumu wa Kumwamba. Okhawo amene akhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ali ndi chikhulupiliro chimene chiwatsogolera ku ntchito ya Mulungu. 
Baibulo likutiuza kuti ndi kuchita kusayeruzika kuitana dzina Lake ndi uchimo mu mtima. Kodi munapitako ku msonkhano wa mapemphero a kuphiri? Ma dikoni ena akazi amafuula ndi kufuula, kuitana dzina Lake chifukwa sanakumane ndi Yesu mu choonadi, kapena kuvomereza Mzimu m’mitima yawo, kapena kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Iwo amaitana dzina Lake mwamphamvu chifukwa akukhala mu mantha aakulu kuti adzapita ku gehena. 
Tilinganize kuti munthu wina amene anapereka moyo wake kuti atumikire mpingo ngati mtumiki oyenda yenda kapena mbusa anakanidwa ndi Ambuye. Kukanidwa ndi makolo kapena mkazi kungakhale kokwanira kuphwanya mtima wa munthu, koma kukanidwa ndi Mulungu, Mfumu ya mafumu, Oweruza wa miyoyo yathu, kodi tizapita kuti? 
Ndi kukhulupilira kuti izi sizidzachitika kwa wina aliyense wa inu. Chonde mverani ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Ndi chifuniro cha Mulungu kuti ife tibadwe mwatsopano ndi kukhala mkati mwa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. 
Ife Akristu tiyenera moona kukhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu ndi kukhala ndi mphamvu mu choonadi cha Baibulo. Pokhapo ndi pamene tingapulumutsidwe ku chiweruzo cha Mulungu.