(Macitidwe a Atumwi 1:4-8)“Ndipo posonkhana nao pamodzi, anawalamulira asacoke ku Yerusalemu, komatu alindire lonjezano la Atate, limene, anati, munalimva kwa Ine; pakuti Yohane anabatizadi ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera, asanapite masiku ambiri. Pamenepo iwowa, atasonkhana pamodzi, anamfunsa Iye, nanena, Ambuye; kodi nthawi yino mubwezera ufumu kwa Israyeli? Koma anati kwa iwo, Sikuli kwa inu kudziwa nthawi kapena nyengo, zimene Atate anaziika m’ulamuliro wace wa Iye yekha. Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ace a dziko.”
Kodi kukhazikika kwa Mzimu Woyera ndi mphatso ya Mulungu kapena kumaperekedwa cifukwa cha kulimbikira kwa munthu?
Ndi mphatso yopatsidwa kwa munthu amene amalandira chikhululukiro cha machimo ake, ndipo ali ndi tanthauzo la kukwaniritsa kwa lonjezo la Mulungu.
Tsiku lina zinandichitikira zolandira malawi a chinthu china ngati Mzimu Woyera kudzera m’mapemphero. Koma malawi amenewa sanakhale nthawi yaitali kwambiri, ndipo mwamsanga anafa chifukwa cha kuchita machimo. Komabe, tsopano ndikufuna ndikuonetseni choonadi cha Mzimu Woyera, umene uzakhala mwa ife kwamuyaya, osati kudzera mwa mzimu wabodza umene umazimitsidwa mophweka ndi uchimo, koma kudzera mu uthenga wabwino oonadi. Mzimu Woyera umene ndikufuna kukuonetsani tsopano kudzera mu uthenga uwu sichinthu chimene mungalandire kudzera m’mapemphero, koma kudzera m’chikhulupiliro chokha mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Ndikufuna ndikutsogolereni kuti mulandire [1]kukhazikika kwa Mzimu Woyera kudzera mu bukuli. Muzazindikira kuti Mzimu Woyera umalimbikitsa uthenga umene ndikupereka kwa inu. Ndi khumbo lalikulu la Mulungu kwa ife kuti tilandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera panthawi ino. Mungaphunzire za kukhazikika kwa Mzimu Woyera ndi kuulandira kudzera mu buku limodzi limeneli. Ngati ili buku ndilosakwanira kwa inu, ndikukupemphani kuti muwerenge mabuku awiri anakhazikitsidwa ndi ine kumbuyoku. Mudzalandira chikhulupiliro changwiro pamaso pa Mulungu kudzera m’mabuku amenewa.
| 1Mzimu Woyera umakhala m’mitima ya obadwa mwatsopano, amene anakhululukidwa machimo awo onse pokhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Pamene wabwera mwa oyera mtima, Umakahala mwa iye kwamuyaya, ndipo sumamusiya iye ngati iye akukhulupilira mu uthenga wabwino. Umapereka chitsimikizo kwa oyera mtima, umawatsogolera kuti adziwe chifuniro cha Mulungu mu Baibulo, kuwalimbitsa kuti agonjetse mayesero ndi zovuta zomwe anabadwa nazo m’dziko lino, ndipo umawalola iwo kubala zipatso za Mzimu zochoruka. Mulungu amalemekeza thupi la oyera mtima monga kachisi wa Mulungu kudzera mu kukhazikika kwa Mzimu Woyera (Macitidwe a Atumwi 2:38-39, Yohane 14:16, 16:8-10, 1 Akorinto 3:16, 6:19, Agalatiya 5:22-23). |
Akristu ambiri akuyesa kulandira Mzimu Woyera monga m’mene unatsikira pa ophunzira a Yesu pa Tsiku la Pentekosite. Anthu ena apeza ndalama zambiri mwa kugwiritsira ntchito njira imeneyi. Iwo amanamizira kuti Mzimu Woyera ndi chinthu chimene chingapezeke kudzera mu mphamvu za munthu. Akufuna kukhala ndi masomphenya, kuchita zodabwitsa, kumvera mawu a Yesu, kuyankhula m’malilime, kuchilitsa matenda ndi kutulutsa ziwanda. Komabe, ali ndi uchimo m’mitima yawo, ndipo akutsogoleredwa ndi mizimu yoipa (Aefeso 2:1-2). Ngakhale tsopano anthu ambiri akupitiliza kukhala opanda kudziwa kuti ali pansi pa mphamvu ya mizimu yoipa. Ndi chifukwa chake Satana amanyengelera ndi kunyenga anthu kugwiritsira ntchito njira za mitundu yonse monga zodabwitsa ndi zoziziwitsa zimene kwenikweni ndi zithunzithunzi chabe.
Yesu analamula ophunzira Ake “asacoke ku Yerusalemu, komatu alindire lonjezano la Atate” (Macitidwe a Atumwi 1:4). Kulandira kwa Mzimu Woyera kunavumbulidwa mu Machitidwe a Atumwi sikudzera mu “zochitikapo,” “kuzipereka” kapena “mapemphero a kulapa,” koma kudzera mu “kuyembekezela kwa lonjezo la Mulungu” la kupereka Mzimu Woyera kwa iwo. Chimene tiyenera kuphunzirapo kuchokera mu ndime imeneyi ndi chakuti kukhazikika kwa Mzimu Woyera sikuchitika kudzera m’mapemphero a anthu. Ndi mphatso ya Mulungu, imene ingapezeke kudzera mu chikhulupiliro chathunthu mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu mokha, umene Mulungu Atate ndi Yesu Kristu anapereka kwa mtundu wa anthu. Kukhazikika kwa Mzimu Woyera koona kumachitika kudzera m’chikhulupiliro cha uthenga umene Yesu Kristu anapereka kwa ife. Mulungu anatipatsa ife choonadi cha madzi ndi Mzimu kotero kuti tilandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera (Yohane 3:3-5).
Mawu akuti “Lonjezo la Mzimu Woyera” amaoneka nthawi zambiri mu Chipangano Chatsopano. Petro amanena mu uthenga wake (Macitidwe a Atumwi 2:38-39) pa ubatizo wa Mzimu Woyera pa Tsiku la Pentekosite, “Ndi lonjezo la Mulungu kupereka Mzimu Woyera kwa iwo amene analandira chikhululukiro cha machimo chifukwa cha kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma.”
Kukhazikika kwa Mzimu Woyera ndi mphatso yoperekedwa kwa iwo amene amalandira chikhululukiro cha machimo awo, ndipo ali ndi tanthauzo la kukwaniritsa kwa lonjezo la Mulungu. Mzimu Woyera m’Chipangano Chatsopano si china chake chomwe chingapezeke kudzera mu mgwirizano pakati pa Mulungu ndi anthu, koma ndi mphatso yolonjezedwa kwa Mulungu. Motero, kukhazikika kwa Mzimu Woyera, monga kunavumbulutsidwa mu Machitidwe a Atumwi, sichinthu chimene chingapezeke kudzera m’mapemphero (Macitidwe a Atumwi 8:19-20).
Mzimu Woyera umabwera pa iwo okha amene akhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu umene Yesu anapereka kwa ife. Yesu analonjeza ophunzira Ake kuti azatumiza Mzimu Woyera kotero kuti akhale ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera. “Pakuti Yohane anabatizadi ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera, asanapite masiku ambiri.” (Macitidwe a Atumwi 1:5). Choncho, ophunzira Ake anayembekezera kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Mulungu.
Mwa kuyang’ana pa zikhulupiliro za iwo ali mu Baibulo amene analandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera, timazindikira kuti zinachitika osati kudzera mu mphamvu zawo koma mwa chifuniro cha Mulungu. Kukhazikika kwa Mzimu Woyera kumene kunabwera pa ophunzira mu Machitidwe a Atumwi sikunachitike chifukwa cha ntchito za munthu kapena kukwaniritsa kwa kuuzimu.
Kubwera kwa Mzimu Woyera pa ophunzira Ake, monga m’mene kunalembedwa mu Machitidwe a Atumwi, posachedwa kunakhala koonadi. Kunali monga m’mene Yesu ananenera, “asanapite masiku ambiri.” Ili linali dalitso loyamba pa nthawi ya mpingo oyambilira. Mwakuyang’ana pa Malemba, tingathe kuona kuti lonjezo la Mulungu silinakwaniritsidwe chifukwa cha kusala kudya, mapemphero kapena kuzipereka-nsembe, koma kudzera mu chikhulupiliro mwa Yesu. Pamene Yesu anakwera kumwamba, okhulupilira analandira chikhululukiro cha machimo ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera pa nthawi imodzi.
Mzimu Woyera Unabwera pa Ophunzira a Yesu Mwadzidzidzi Kuchokera Kumwamba!
“Ndipo pakufika tsiku la Pentecoste, anali onse pamodzi pa malo amodzi” (Macitidwe a Atumwi 2:1). Ophunzira a Yesu anasonkhana pamodzi pomwe anali kuyembekezera kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Mulungu la kuwatumizira Mzimu Woyera. Ndipo Mzimu Woyera pomaliza unatsikira pa iwo.
“Ndipo mwadzidzidzi anamveka mau ocokera Kumwamba ngati mkokomo wa mphepo yolimba, nadzaza nyumba yonse imene analikukhalamo. Ndipo anaonekera kwa iwo malilime ogawanikana, onga amoto; ndipo unakhala pa iwo onse wayekha. Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa” (Macitidwe a Atumwi 2:2-4).
Mzimu Woyera unabwera pa iwo “mwadzidzidzi kuchokera Kuwamba.” Apa mawu akuti “mwadzidzidzi” akutanthauza kuti kunachitika osati mwa chifuniro cha munthu. Kuonjezerapo, mawu akuti “kuchokera Kumwamba” akufotokoza kumene Mzimu Woyera unachokera, ndiponso kutsutsa nzeru yakuti kukhazikika kwa Mzimu Woyera kungapezeke kudzera mu chifuniro cha munthu kapena mphamvu. Mawu akuti, “kuchokera Kumwamba” amaonetsa kuti kunena kuti Mzimu Woyera ungapezeke kudzera mu mapemphero ndi kunena kwachinyengo.
M’kulankhula kwina, kunena kuti Mzimu Woyera unatsika mwadzidzidzi kuchokera Kumwamba kukutanthauza kuti kukhazikika kwa Mzimu Woyera sikuchitika kudzera mu zinthu za padziko lapansi, monga kuyankhula m’malilime kapena kuzipereka-nsembe. Ophunzira a Yesu poyamba anayankhula m’malilime kuti alalikire uthenga wabwino okoma ku anthu a ku maiko onse. Chifukwa cha chimenechi chinali chakuti alole iwo kulalikira uthenga wabwino mu chilankhulo chachilendo chimene anali kulankhula Ayuda m’chilankhulo chawo kudzera mu thandizo la Mzimu Woyera. Anthu a kumaiko onse anaganiza kuti kunali kodabwitsa kuona ophunzira akuyankhula m’malilime mu zilankhulo zawo, chifukwa ophunzira ambiri anali a ku Galileya
“Ndipo anaonekera kwa iwo malilime ogawanikana, onga amoto; ndipo unakhala pa iwo onse wayekha wayekha. Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera” (Macitidwe a Atumwi 2:3-4). Apa tiyenera kumvetsetsa mawu akuti, Mzimu Woyera “unakhala pa iwo onse wayekha wayekha.” Ophunzira, akuyembekezera kubwera kwa Mzimu Woyera pamalo amodzi, anakhulupilira kale mu uthenga wabwino wa kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.
Akristu ambiri masiku ano samvetsetsa mbali ya ndime imeneyi, akukhulupilira kuti kubwera kwa Mzimu Woyera kumachitika ndi mawu ngati kuomba kwa mphepo pamene akupemphera. Komabe, uku ndi kusamvetsetsa pa za Mzimu Woyera kumene kumabwera kuchokera ku umbuli ndi kusokonezeka. Kodi Mzimu Woyera umapanga phokoso lotero pamene ukubwera pa anthu? Ai, Sumachita zimenezo.
Zimene anthu amamvera ndi makutu awo ndi phokoso limene Satana amapanga pamene akuononga miyoyo ya anthu. Amapanga phokosoli pamene akugwira ntchito mwa chinyengo, mawu otsanzira ndi zozizwitsa zabodza ndi mphamvu za kuti akakamize anthu kukhala mu chisokonezo ponamizira ngati ndi Mzimu Woyera. Anthu amalakwitsa zinthu zimenezi pakutsimikiza za kubwera kwa Mzimu Woyera. Anthu akuganizanso kuti Mzimu Woyera umabwera ndi “Suihhh~” phokoso ngati la mphepo yamphamvu. Iwo akunyengedwa ndi ziwanda. Kubwera kwa Mzimu Woyera monga kunalembedwa mu Machitidwe a Atumwi kunakwanitsidwa kudzera mu kukhulupilira kokha mu uthenga wabwino okoma.
Chikhulupiliro cha Petro (1 Petro 3:21) chinali changwiro chokwanira kulola iye kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera.
Kukongoletsa chochitika cha pa Pentekosite oyambilira mu Machitidwe a Atumwi 2, Mulungu akufuna kutsindika pa choonadi chakuti Mzimu Woyera unabwera pa iwo chifukwa anakhulupilira kale mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Koma anthu nthawi zambiri amaganiza za “Pentekosite” ngati nthawi imene Mzimu Woyera umabwera kuchokera kumwamba ndi zizindikiro zauzimu ndiponso chipwirikiti.
Ndi chifukwa chake masiku ano mu misonkhano yachitsitsimutso, kuli chikhulupiliro cha kuti munthu angalandire Mzimu Woyera kudzera mu mapemphero amphamvu, kusala kudya, kapena kuika manja. Chochitika chotere monga kukhala ndi ziwanda, kukhala opanda mphamvu kugwera mumasomphenya kwa masiku ambiri, kapena kunjenjemera mosagwirika sinchito za Mzimu Woyera.
Mzimu Woyera uli wanzeru ndipo susamala za m’mene munthu alili. Sumaonetsa kukwiya kwa munthu chifukwa Iye ndi Munthu wa Mulungu amene ali ndi nzeru, chikumbumtima ndi chifuniro. Umabwera pa anthu pokhapo pamene akhulupilira mu mawu a uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu (Machitidwe a Atumwi 2:38).
Petro anachitira umboni kuti Mzimu Woyera unabwera pa ophunzira monga ananeneratu mneneri Yoweli. Kunali kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Mulungu, limene linanena kuti Mzimu Woyera udzagwera pa iwo amene adzalandira chikhululukiro cha machimo awo. M’mawu ena, kukhala kwa Mzimu Woyera kuperekedwa kwa iwo amene akhulupilira mu choonadi chakuti Yesu anabatizidwa ndi Yohane ndipo anapachikidwa kuti apulumutse mtundu onse wa anthu ku machimo awo. Ulaliki wa Petro, pamodzi ndi uneneri wa Yoweli, zikuonetsa kuti tiyenera kudziwa chifukwa chimene Yesu anabatizidwira ndiponso chifukwa chomwe tiyenera kukhulupilira mwa iwo. Kudziwa choonadi chimenechi kumatsogolera Akristu kulandira Mzimu Woyera.
Kodi mumakhulupilira mu uthenga wabwino okoma umene Petro anachitira umboni? (1 Petro 3:21) Kapena kodi mudakali ndi zikhulupiliro zopanda ntchito komanso zabodza zimene ndi zosafunika konse ku uthenga wabwino okoma? Kodi mukuyesa kulandira Mzimu Woyera kudzera mu zimene mukuchita panokha mosasamala kanthu za chikonzero cha Mulungu? Ngakhale kuti wina amakhulupilira mwa Mulungu ndi kupemphera mapemphero a kulapa ndi chiyembekezo chakuti akutsuka machimo awo, palibe njira ina yolandilira kukhazikika kwa Mzimu Woyera koposa kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Kodi mukuyembekezabe kukhazikika kwa Mzimu Woyera, ngakhale mulibe chidziwitso cha uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu? Kodi mukudziwa tanthauzo loona la ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda, limene limapangitsa Mzimu Woyera kukhala m’mitima yanu? Muyenera kudziwa kuti kukhazikika kwa Mzimu Woyera kumatheka pokhapo ngati mwakhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Kukhazikika koonadi kwa Mzimu Woyera kungaloledwe kwa okhwao amene akhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. Tikuyamika Mulungu pakutipatsa uthenga Wake wabwino wa madzi ndi Mzimu, umene ukutilola kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera.