• All e-books and audiobooks on The New Life Mission website are free
  • Explore multilingual sermons in global languages
  • Two new revised editions in English have been released
  • Check out our website translated into 27 languages
Search

Sermons

Mutu 8: Mzimu woyera

[8-2] Kodi WinaWake Angathedi Kugula Mzimu Woyera Mwa Kulimbikila Kwake? (Macitidwe a Atumwi 8:14-24)

Kodi WinaWake Angathedi Kugula Mzimu Woyera Mwa Kulimbikila Kwake?(Macitidwe a Atumwi 8:14-24)
“Koma pamene atumwi a ku Yerusalemu anamva kuti Samariya adalandira mau a Mulungu, anawatumizira Petro ndi Yohane; amenewo, m’mene adatsikirako, anawapempherera, kuti alandire Mzimu Woyera: pakuti kufikira pamenepo nkuti asanagwe pa wina mmodzi wa iwo; koma anangobatizidwa m’dzina la Ambuye Yesu. Pamenepo anaika manja pa iwo ndipo analandira Mzimu Woyera. Koma pakuona Simoni kuti mwa kuika manja a atumwi anapatsidwa Mzimu Woyera, anawatengera ndalama, nanena, ndipatseni inenso ulamuliro umene, kuti amene ali yense ndikaika manja pa iye, alandire Mzimu Woyera. Koma Petro anati kwa iye, Ndalama yako itayike nawe, cifukwa unalingirira kulandira mphatso ya Mulungu ndi ndalama. Ulibe gawo kapena colandira ndi mau awa; pakuti mtima wako suli wolunjika pamaso pa Mulungu. Cifukwa cace lapa coipa cako ici, pemphera Ambuye, kuti kapena akukhululukire iwe colingirira ca mtima wako. Pakuti ndiona kuti wagwidwa ndi ndulu yowawa ndi singa ya cosalungama. Ndipo Simoni anayankha nati, Mundipempherere ine kwa Ambuye kuti zisandigwere izi mwanenazi.”
 

Kodi munthu angalandire Mzimu Woyera mwa kuika manja?
Ayi. Iye ayenera kukhulupilira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.

Moyang’ana pa ndime yaikukulu, ndifuna ndipereke uthenga wakuti ngati “wina angalandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera kudzera mu kulimbikila kwake.” Atumwi pa nthawi ya Mpingo woyamba analandira mphamvu kwa Mulungu ndipo anatumidwa ku malo osiyana siyana ndi Iye. Muli zinthu zochitika zodabwitsa zochuluka mu Machitidwe a Atumwi, imodzi mwa izo ndi Mzimu Woyera kutsikira pa okhulupilira pamene Atumwi anaika manja awo pa mitu yawo. Baibulo limati, “Pamene atumwi anaika manja awo pa aja amene anali asanalandire Mzimu Woyera ngakhale kuti anali kukhulupilira mwa Yesu, iwo analandira Mzimu Woyera.”
Ndiyeno kodi analandira bwanji Mzimu Woyera kudzera mu kuika manja? Pa nthawi imeneyo mawu a Mulungu anali adakali kulembedwa ndipo ntchito inali isanathe kweni kweni, choncho Mulungu anapatsa Atumwi ake mphamvu zapadera dera kuti achite ntchito Yake. Iye anali ndi Atumwi ndipo anachita zodabwitsa komanso zozizwitsa zochuluka kupitira mwa iwo. Inali nthawi ya padera dera, pamene Mulungu anali kuchita zozizwitsa ndi zodabwitsa zimene zinali kuoneka ndi diso la munthu n’cholinga chakuti apangitse anthu kukhulupilira kuti Yesu Kristu ndi Mwana wa Mulungu komanso Mpulumutsi. Panali chifunikiro cha Mulungu, pamodzi ndi Atumwi, kuti aonetse mwa mphamvu ntchito ya Mzimu Woyera kuti atsimikizire kuti Yesu Kristu ndiye Mulungu ndipo kuti Iye ndi Mwana wa Mulungu, Mpulumutsi. Kukanakhala kuti Mzimu Woyera sunagwire ntchito kupitira mwa zodabwitsa ndi zosakhulupililika pa nthawi ya mpingo woyamba, panalibe anakakhulupilira kuti Yesu ndi Mpulumutsi. 
Ngakhale ziri choncho, sichoyenera kwa ife kuti tilandire Mzimu Woyera kudzera mu zozizwitsa zooneka ndi zodabwitsa lero, chifukwa chakuti Baibulo linamalizika. M’malo mwake, kukhazikika kwa Mzimu Woyera tsopano kwakhala m’chikhulupiliro. Kulankhula kwina, mwakukhulupilira mu uthenga wabwino wa Choonadi. Mulungu amapereka kukhazikika kwa Mzimu Woyera kwa iwo amene ali ndi chikhulupiliro mu uthenga wabwino wa Choonadi pamaso pa Mulungu. Kukhazikika kwa Mzimu Woyera kumachitikira iwo okha amene akhulupilira mawu a Mulungu, pamene kunakwaniritsidwa ndi kubwera kwa Yesu pa dziko lino mwa ubatizo Wake ndi mwazi. 
Masiku ano, abusa ambiri amaphunzitsa okhulupilira kuti zochitika zowoneka za zodabwitsa ndiye zizindikiro za kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Ndipo amatsogolera okhulupilira kuti alandire Mzimu Woyera m’njira yomweyi. Amanyenga anthu powapatsa ziphunzitso zabodza, monga mwakuti kulankhula m’malilime ndi chizindikiro cha kubwera kwa Mzimu Woyera. Abusa amenewa amaziona iwo kukhala atumwi amene amachita zinthu zodabwitsa ndi zozizwitsa zazikulu, ndipo amakoka chidwi cha achipembedzo otentheka amene amafuna kudziwa Mulungu kudzera mu zokumva zawo. 
Chinyengochi chafalikira ku Akristu ambiri padziko lonse, ndipo ambiri mwa iwo atsatira zikhulupiliro zawo ndi kulandira mizimu yoipa kupitira mwa njira yauzimu. Ngakhale tsopano, anthu amene anatengeka ndi chinyengo cha chipembedzo amaganiza kuti iwo angapangitse ena kuti alandire Mzimu Woyera kudzera mu kuika kwa manja. 
Ngakhale tero, kukhala onyengedwa ngati Simoni, iwo ali ngati wamatsenga yemwe waonekera m’ndime yaikulu. Iwo ndi wolezela ndi chikhutilitso cha iwo wokha ndi umbombo wa zinthu, koma zochita zawo zonse zimangodzetsa chisokonezo pakati pa anthu. Mtundu wotere wa chiphunzitso chabodza umachokako kunjira yoona yolandirira kukhazikika kwa Mzimu Woyera pamaso pa Mulungu. 
Ngakhalenso masiku ano, aneneri ambiri onyenga amagwira ntchito za Satana kudzera mu zochita zawo zolakwika za chipembedzo, kunamizira kuti akugwira ntchito ya Mzimu Woyera. Akristu Woona ayenera kukakamira ku mawu a Mulungu, nzeru zimene ndi njira yokhayo yolandiriramo kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Otchedwa Achipentekosite, amene amakakamira kwambiri pa zinthu zoziona kuthupi za Mzimu Woyera, ayenera kutaya zikhulupiliro zawo zopanda pake, abwerera ku mawu a Mulungu ndi kukhulupilira mu choonadi, chimene mosimikizika chidzawatengera ku kukhazikika kwa Mzimu Woyera. 
Simoni anali wamatsenga wotchuka mu Samaliya pa nthawiyo. Ataona ophunzira a Yesu akupangitsa anthu kuti alandire Mzimu Woyera, iye anaganiza za kuti agule Mzimu Woyera ndi ndalama. Anthu amene ali ndi chikhulupiliro chotere mwachidziwikire anakhala akapolo a Satana, kugwiritsidwa nchito ndi iye kugwira ntchito yake. Simoni anali kufuna kuti alandire Mzimu Woyera koma khumbo lake silinali china kuposa umbombo. Tingathe kuona kuti chikhulupiliro cha mtundu wotere si chikhulupiliro choona cholandilira Mzimu. 
Simoni anali kufuna kugula Mzimu Woyera ndi ndalama chifukwa cha umbombo wake wakufunitsitsa mphamvu Zake. Iye anadzudzulidwa mwankhanza ndi mtumiki wa Mulungu, Petro, pa chifukwachi. Ngakhale kuti kunanenedwa kuti Simoni anali kukhulupilira mwa Yesu, iye sanali munthu amene analandira Mzimu Woyera kudzera mu chikhululukiro cha machimo. Mkulankhula kwina, iye anaganiza kuti anakatha kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera mwakupereka zinthu za padziko kwa Mulungu. 
Ngakhale kuti maonekedwe ake akunja analikuonetsa kuti anali munthu wokhulupilira mwa Yesu, maganizo ake a mkati sanali ogwirizana ndi mawu a Yesu oona. Mmalo mwake, iye anadzadzidwa ndi dyera lakuthupi. Petro, amene anadziwa maganizo a Simoni, anamdzudzula pakufuna kugula Mzimu Woyera ndi ndalama, umene uli mphatso ya Mulungu. Iye anauza Simoni kuti adzafa ndi ndalama zake. 
Masiku ano, aneneri onyenga ogwidwa ndi mizimu yoipa amafuna kunyenga anthu bodza mwakuwapangitsa kuganiza kuti zodabwitsa zonse ndi zozizwitsa ndi ntchito za Mzimu Woyera. Tingathe kuona anthu amene amasilira mphamvu yotere ndi kupemphera mwamphamvu kuti alandire Mzimu Woyera. Ngakhale tero, munthu ayenera kukhala nacho m’maganizo kuti palibe amene angalandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera kupitira mwa mapemphero opempheredwa mwa umbombo wake wa dziko. 
Kodi alipo anthu achikoka pafupi ndi inu mwa mpata wina uliwonse? Muyera kukhala tcheru ndi anthu oterewa. Iwo amafika kwa ena ndi chikhulupiliro chotentheka. Iwo amanena kuti angachotse ziwanda ndiponso kupangitsa anthu kuti alandire Mzimu Woyera kudzera mu kuika manja awo. Komabe, iwo alibe mphamvu ya Mzimu Woyera, koma mphamvu za mizimu yoipa. Iwo amene amabvomereza kuti analandira Mzimu Woyera mwanjira yoikidwa manja akuzitsogolera iwo wokha ndi ena kulandira mizimu yoipa basi. 
Kukhazikika koona kwa Mzimu Woyera kumabwera pa iwo amene akhulupilira mu mawu a madzi ndi Mzimu (1 Yohane 5:3-7). Ngakhale kuti uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndiwolembedwa momveka bwino mu Baibulo, chifukwa chakuti anthu ambiri ali ndi tchimo m’mitima yawo, iwo amafuna kufika kwa Mulungu kupitira mu mphamvu zauzimu ndi zooneka ndi maso monga maloto, kulankhula m’malilime, kuona zamtsogolo ndi kutulutsa ziwanda. Ichi ndicho chifukwa aneneri onyenga amatha kunyenga anthu ambiri kuti akhulupilire mu Chikristu chamatsenga chochokera kwa mdierekezi. 
Petro anadzudzula Simoni ponena kuti; “Ndalama yako itayike nawe, cifukwa unalingirira kulandira mphatso ya Mulungu ndi ndalama. Ulibe gawo kapena colandira ndi mau awa; pakuti mtima wako suli wolunjika pamaso pa Mulungu. Cifukwa cace lapa coipa cako ici, pemphera Ambuye, kuti kapena akukhululukire iwe colingirira ca mtima wako. Pakuti ndiona kuti wagwidwa ndi ndulu yowawa ndi singa ya cosalungama.” Tiyenera kupuma mobuula ndi chisoni pachoona chakuti kuli atumiki ochuluka ngati amenewa masiku ano. Ambiri mwa awa ndi anthu achikoka. Iwo amafuna ndalama ku nkhosa zawo. Tiyenra kukhala otalikana ndi chikhulupiliro cha mtundu uwu ndi kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera pokhulupilira mu uthenga wabwino woona wa madzi ndi Mzimu. (Mateyu 3:15, 1 Petro3:21, Yohane 1:29, Yohane 19:21-23).
 
 

Anthu achikoka amagwira ntchito kudzera mu kuika manja!


Tiyenera kukhala kutali ndi chikhulupiliro cha mtundu uwu. Anthu ena masiku ano ali ndi chikhulupiliro chopanda pake chakuti iwo angalandire Mzimu Woyera ngati alandira kuika kwa manja kuchokera kwa iwo amene anakhala ndi mphamvu. Iwo amaganiza kuti pakuti Malemba amanena kuti anthu ambiri analandira Mzimu Woyera pamene anaikidwa manja kuchokera kwa Atumwi, kuti nawonso angachitenso choncho. Onamizira ena nawonso ali ndi chikhulupiliro chopanda pake chimenechi kuti iwo angapatse anthu kukhazikika kwa Mzimu Woyera kudzera mwa kuika manja awo. Tiyenera kukhala ozindikira za kukhalapo kwa anthu amenewa. 
Komabe, tiyenera kukhala nacho m’maganizo kuti chikhulupiliro chawo ndi chosiyana kwambiri ndi chija cha Atumwi mu nthawi ya Mpingo woyamba. Masiku ano chopsinja chokhwima kwambiri ku zikhulupiliro za Akristu ena ndi chakuti iwo alibe chikhulupiliro mu uthenga wabwino woona wa madzi ndi Mzimu. Iwo amanena kuti amakhulupilira mwa Mulungu, koma salemekeza Iye ndipo m’malo mwake amazinyenga okha ndi ena. Choncho, ochimwa sangalandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera kapena kupangitsa ena kutero. Ngati munthu wina wanena kuti Mzimu wina unabwera pa wochimwa, mzimuyu siunalidi Mzimu Woyera; koma unali mzimu wa Satana wongozinamizira kukhala Mzimu woona. 
Atumwi mu nthawi ya mpingo woyamba anali anthu amene anali kudziwa ndi kukhulupilira kuti Yesu Kristu anali Mpulumutsi, amene anachotsa machimo onse a mtundu wa munthu kudzera mu ubatizo Wake ndi Yohane ndi imfa Yake pa Mtanda. Iwo anatha kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera chifukwa anali kukhulupilira mu choonadi cha ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda. Iwo analalilikiranso uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ku anthu ena, motero kuwathandiza kuti alandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera. 
 Koma masiku ano, Akristu ambiri ali ndi zikhulupiliro zolakwika. Kodi ndi chothekadi masiku ano kwa wochimwa kuti alandire Mzimu Woyera kudzera mu kuika kwa manja kuchokera kwa mlaliki wochimwanso? Icho ndi chopanda nzeru kotheratu. Pali omwe amanena kuti ngakhale kuti ali ndi tchimo m’mitima yawo, iwo analandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Ngakhale kuti munthu wina aoneka ngati mbusa wabwino m’maso mwa omukhulupilira ake, iye sangapangitse wina aliyense kuti alandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera ngati mu mtima mwake muli uchimo. 
Ngakhale zili choncho, anthu ambiri ali ndi mtundu wa chikhulupiliro cholakwika chotere. Ichi ndiye chifukwa aneneri ambiri onyenga amakwanitsa kutengera anthu ku gahena. Muyenera kudziwa chilungamo kuti iwo amene amaphunzitsa chikhulupiliro chotere ndi aneneri onyenga. Awa ndi anthu amene anagwidwa kale ndi ziwanda. 
Ngati munthu ali ndi chimo mu mtima mwake, kodi Mzimu Woyera ungakhale mwa iye? Yankho ndi ai. Kenako kodi ndi chotheka kuti munthu amene ali ndi tchimo mu mtima mwake apangitse ena kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera? Kachiwiri, yankho ndi ai. Ndiye kodi ndi chiani chimene chimapangitsa anthu achikoka masiku ano kuti azichita zodabwitsa ndi zozizwitsa mu Chikristu, pamene adakali ndi uchimo mu mitima yawo? Ndi mizimu zoipa zimachita choncho. Mzimu Woyera siungakhale mkati mwa wochimwa. Iye amakhala mwa aja ali ndi chikhulupiliro mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu okha. Kodi mukutsimikiza kuti mzimu umene unabwera pa inu ndi Mzimu Woyera? 
Mu Yohane 3:5, Yesu anati, “Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu.” Motero, kukhazikika kwa Mzimu Woyera kungapatsidwe mwakukhulupilira mu uthenga wabwino woona wa madzi ndi Mzimu. Kulakwitsa kumene Akristu ambiri amapanga masiku ano ndi kukhulupilira kuti munthu angalandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera mwakulandira kuika kwa manja kwa atumiki ochimwa. Uku ndi kulakwitsa kwakukulu. Masiku ano Akristu ambiri ndi atumiki ali ndi chikhulupiliro ndi chitsimikizo kuti kukhazikika kwa Mzimu Woyera kumabwera pa iwo kudzera mwa kuika manja.
 
 

Mgwirizano pakati pa chikhululukiro choona cha machimo ndi kuika kwa manja


 “Kuika kwa manja” ndi njira imene wina angaperekere chinthu chili mkati mwake ku chinthu chinacho. Chiganizireni m’njira iyi: Ngati talankhula mu maikolofoni, mawu amapita mu nthambo kukalowa mu chimkuzamawu ndipo kenako kutulukira ku chotulutsira mau okweza kuti wina aliyense amvere. Mofanana, mu Chipangano Chakale, pamene wochimwa ankaika manja ake pa mutu pa nsembe, machimo ake anali kuperekedwa pa nsembeyo ndipo motero anali kukhululukidwa. M’njira imodzi modzi, mphamvu ya Mulungu imapita ku anthu ngati atumiki Ake aika manja pa iwo. Mnjira imeneyi, kuika kwa manja kwatenga tanthauzo la “kupatsira, kusamutsa.”
Anthu achikoka samapangitsa anthu kuti akhale ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera kudzera mu kuika manja awo, koma m’malo mwake amawapangitsa kuti alandire mizimu yoipa. Muyenera kukumbukira kuti munthu amene ali ndi mphmvu ya mizimu yoipa amapatsira mizimuyo kwa ena kudzera mu kuika manja. Ngati munthu wogwidwa ndi chiwanda aika dzanja lake pa mutu pa wina, chiwanda chomwe chili mwa iye chimapita mwa munthuyo, chifukwa Satana amagwira ntchito kudzera mwa ochimwa. Pachifukwa ichi, aliyense ayenera kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ngati afuna kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Satana amalamulira iwo amene ali mu uchimo, ngakhale kuti amakhulupilira mwa Yesu, ngati iwo alephera kulandira chikhululukiro cha machimo. 
 Ngati munthu wina waikidwa manja ndi munthu wogwidwa ndi ziwanda, ziwanda zizabweranso kwa iye ndipo nayenso azachita zodabwitsa zabodza. Tifunika kudziwa kuti ziwanda zimalowa mwa ena kudzera mu kuika manja, ndiponso kuti kukhazikika kwa Mzimu Woyera ndi kotheka pokhapo kudzera mu chikhulupiliro cha uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. 
Kuika manja ndi njira yopangidwa ndi Mulungu yopatsira chinthu ku china. Koma Satana amapangitsa anthu ambiri kuti alandire mizimu yoipa kudzera mu kuika kwa manja. Choona ndi chakuti masiku ano pali anthu ambiri amene amafuna kugula mphamvu ya Mzimu Woyera ndi ndalama ndi bvuto lalikulu. 
 
 

Akristu ambiri samvetsetsa choonadi cha kukhazikika kwa Mzimu Woyera


Akafunsidwa kuti angalandire motani kukhazikika kwa Mzimu Woyera, anthu ambiri amayankha kuti ndi chotheka kudzera m’mapemphero akulapa kapena kusala chakudya. Ichi si choona. Kodi Mzimu Woyera umadza pa inu mukapereka mapemphero a padera dera kwa Mulungu? Ai. Kukhazikika kwa Mzimu Woyera kumabwera pa okhawo amene akhulupirira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. 
Chifukwa Mulungu ndi choona, Iye anapanga lamulo lolandilira kukhazikika kwa Mzimu. Kodi Mzimu Woyera ungakhale mwa munthu amene ali ndi tchimo mu mtima mwake? Yankho ndilodziwikiratu kuti ai. Munthu sangalandire Mzimu Woyera kudzera mu kuika kwa manja. Ngakhale kuti munthu wina amapita ku misonkhano ya chitsitsimutso ndi kupemphera kwa Mulungu moona mtima kuti alandire mphamvu ya Mzimu Woyera, Mzimu Woyera, uzakhalabe kutali ndi iye. Ndichooneka poyera kuti ochimwa sangalandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Ochimwa angalandire kukhazikika koona kwa Mzimu Woyera ngati mphatso, koma pokhapo atalandira chikhululukiro cha machimo pokhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. 
Aliyense amene sadziwa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu sangalandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Masiku ano uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ulikufalikila kwambiri kupitira m’zolemba za Chikristu, misankhano ya mpingo, intaneti, ngakhalenso mabuku a pa intaneti pa dziko lonse. Motero, aliyense amene akufuna-funa uthenga wabwino woona angathe kukhulupilira mwa iwo ndi kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Ngati simunalandirebe kukhazikika kwa Mzimu Woyera, muyenera kuzindikira kuti muchite choncho muyenera kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. 
 

Chitsanzo chachikulu cha chikhulupiliro chabodza!

Masiku ano tikapenyetsetsa zotuluka za anthu amene amalandira mizimu yabodza tingathe kuona kukhalapo kweni kweni kwa ziwanda. “Misonkhano ya chitsitsimutso ya Mzimu Woyera” ndi misonkhano imene anthu amafunitsitsa kulandira Mzimu Woyera. M’misonkhano imeneyi timaona anthu akuomba m’manja ndi kupemphera mapemphero akulapa kwinaku akulira ndi kusala chakudya. Wolalilkira amawaphunzitsa kupemphera mapemphero otentheka pakuwauza kuti Mzimu Woyera sungabwere kufikira atatero. Kenako anthu amafuula mokweza kuti, “Ambuye!” ndi kuyamba mapemphero awo otentheka. 
Kodi anthu otenthekawa angalandire Mzimu Woyera m’njira imeneyi? Ai. Mungaone anthu akufuula ndi kugwera kumbuyo, kenako n’kunjenjemera, kwinaku akupanga mapokoso osadziwika bwino bwino pa misonkhano yotere. Ena akugwera kumbuyo ndi kunjenjemera pansi apa ndi apo, ndipo timaona akufuula ndi kuyamba kulankhula m’malilime. Munthu wina mu m’somkhanowo anafuula mpaka mutu kuwawa ndipo ena anakhuzidwa kwambiri. Ena mwa iwo amayamba kunjenjemera, kugwedezeka paliponse ndi kulankhula m’malilime. Anthu amanena kuti zochitika zimenezi ndi chidziwitso kuti Mzimu Woyera wabwera pa iwo. Koma ganizirani chimene chimachitika ngati chiwanda chikugwira ntchito yache? Kodi iyi ndi nchito ya Mzimu Woyera? Ndizodzwikiratu kuti ai. 
 

Satana amanyenga Akristu ambiri 

Masiku ano, Akristu ambiri amakhala mtundu wa miyoyo ya chipembezo imene Satana amafuna. Satana amanyega anthu ambiri pakuwauza kuti iwo ayenera kuikidwa manja ndi mtumiki wamphamvu kuti alandire Mzimu Woyera. Akristu ambiri amakhulupilira ichi kukhala ngati chiphunzitso choyenera. Satana nayenso amaikamo maganizo m’mitu ya anthu kuti iwo azalandira Mzimu Woyera ngati apemphera moonjezera. Satana wakhala akuyesa yesa kuti achulukitse kawili ndi katatu nambala ya anthu amene ali ndi chikhulupiliro chotere. 
 Choncho, anthu ambiri sadziwa, ndipo sayesa ndi pang’ono pomwe kuphunzira za uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Tiyenera kulimbana naye kuti tipewe maganizo amene Satana amafuna kuika m’mitu yathu ndi kudziwa komanso kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. kukhazikika kwa Mzimu Woyera kumabwera pa iwo okha amene akhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Muyenera kukhulupilira mu zimenezi. 
 

Kusamvetsetsa kwa Akristu pa za kukhazikika kwa Mzimu Woyera
 
Choyamba pa zonse, pali kusamvetsetsa kwakukulu mu zikhulupiliro za otsatira ambiri a Chikristu chachikoka. Iwo amayesa kulandira Mzimu Woyera pamene ali ndi tchimo m’mitima yawo. Amakhulupilira molakwika kuti ngakhale ali ndi tchimo m’mitima yawo, iwo azakwanitsa kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Komabe, munthu wopanda chikhulupiliro chilichonse mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu sangalandire kudzadza kwa Mzimu Woyera. 
Chachiwiri, kunanenedwa kuti mwano wa anthu ndiye umawatchingiriza kuti alandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Nanga kodi ichi chitanthauza kuti wina angalandire Mzimu Woyera ngati sachita mwano? Kodi muli munthu m’dziko lino amene sali wodzikuzaka pang’ono? Munthu wodzikuza amene sangakhululukidwe ndi Mulungu ndi uja amene amaika maganizo ake ku mawu a Mulungu. Anthu ambiri amafuna kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera kudzera mu njira zawo, kukana uthenga wabwino woona wa madzi ndi Mzimu. Choncho, kukhazikika kwa Mzimu Woyera kumabwera pa okhawo amene akhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. 
Chachitatu, kunanenedwa kuti kukhazikika kwa Mzimu Woyera kumadza ngati munthu poyera avomereza machimo ake onse pamaso pa Mulungu. Choncho amalimbikitsidwa kuti avomereze machimo awo ngati afuna kulandira Mzimu Woyera. Koma mufunika kukumbukira kuti kukhazikika kwa Mzimu Woyera sikumadza mophweka ngati munthu angavomereze machimo ake. Akristu ochuluka kwambiri masiku ano amafunitsitsa mwachiyembekezo kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera ndi kudzadza Kwake koma sangalandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera chifukwa aakali ndi tchimo m’mitima yawo. Munthu amene ali ndi khumbo lopupuluma la mtundu uwu azagwidwa ndi ziwanda. 
Chachinayi, ena amati kukhazikika kwa Mzimu Woyera kungapatsidwe ngati molimbika tapempha Mulungu kuti atipatse dalitso limenelo. Koma sikungatengedwe kudzera mu kupempha. Uku ndi kuganiza kolakwika chabe. 
Chachisanu, ena amazindikira kukhazikika kwa Mzimu Woyera pokhala ndi mphamvu zina zauzimu. Kulankhula m’malilime ndiye kumatengedwa kwambiri ngati chidziwitso cha kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Koma Mzimu Woyera siumakhala mu mtima wa munthu chifukwa chakuti iye akutha kutulutsa ziwanda m’dzina la Yesu kapena kulankhula m’malilime achilendo. Tchimo ndi la Satana. Kodi munthu amene ali ndi tchimo mu mtima mwake anganene moonadi kuti walandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera chifukwa chakuti wakhala ndi mphamvu zodabwitsa? Kachikenanso, mchitidwe uwu umachitidwa ndi ziwanda. 
Uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu umene Yesu anatipatsa ndi uthenga wabwino okhawo woona umene ungatitengere kokalandira kukhala kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Ngati mukuganizabe kuti mungalandire Mzimu Woyera ndi chikhululukiro cha machimo kudzera m’njira zina, ndinu osocheletsedwa kwambiri. Ndikhulupilira kuti muzadzimasula nokha ku zikhulupiliro zanu zolakwika ndipo m’malo mwake mudzakhala ndi maganizo auzimu ndi chikhulupiliro cholungama.
Sikuwonjezera kunena kuti masiku ano Akristu ambiri ndiwogwidwa ndi ziwanda. Akristu ambiri adziko lonse amadza pansi pa mphamvu ya ziwanda chifukwa iwo akufuna kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera kupitira mu misonkhano ya chitsitsimutso kapena kuikidwa manja. Iwo amapita kwa anthu ena ake monga woyang’anira nyumba za mapemphero, adikoni akulu akulu othandizira, achitsitsimutso, kapena abusa amene alankhulidwa kuti analandira mphamvu ya Mzimu Woyera. Amapita kwa iwo m’ziyembekezo zolandira Mzimu Woyera kudzera mu kuika manja. Komabe, palibe amene angalandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera kudzera mu chikhulupiliro cha mtundu uwu, ngakhale angakhulupilire mwa Yesu molimbika chotani. Mkulankhula kwina, palibe wina kupatulako Mulungu amene angapangitse munthu kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera. 
Ngati Simoni, anthu ambiri masiku ano amafuna kugula Mzimu Woyera. Iwo amayesa kulandira Mzimu Woyera mwakukhulupilira mu ziphunzitso za dziko, osati uthenga wabwino. Akristu ochuluka padziko lonse ndiwogwidwa m’maganizo otere. Mzimu Woyera umadza pa okhawo amene ali ndi zofunikira zoyenera kuti amulandire Iye. Njira yokhayo yolandiliramo Mzimu Woyera ndi mwakukhulupilira mu uthenga wabwinbo wa madzi ndi Mzimu ndipo ili ndilo yankho lokhalo la choonadi (Machitidwe a Atumwi 2:38).
Kulandira Mzimu Woyera kudzera mu kuika manja kunali kotheka kwa nthawi yochepa yokha pa nthawi ya Mpingo woyamba. Pambuyo pa izi kukhazikika kwa Mzimu Woyera kunadza pa anthu pa nthawi imodzi ndiponso pamene anadziwa ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Choncho, china choposa ntchito ya Mzimu Woyera umene ukuonekera kudzera m’chikhulupiliro m’mawu a Mulungu, china chilichonse ndi ntchito ya ziwanda. Mulungu amati ziwanda ndi atumiki a Satana, ndipo Satana wagwira ntchito mochenjera m’njira ina yake mwakuti anthu sangalandire chikhululukiro cha chimo ngakhale akhulupilira mwa Yesu. Satana amanena bodza kwa anthu ponena kuti iye azawapatsa Mzimu Woyera ngati akhulupilira mwa Yesu ndi kuikidwa manja. Satana amakuza malo ake padziko lonse kudzera m’chinyengo chotere. 
Tsopano tizayang’ana pa zionetsero za iwo ogwidwa ndi ziwanda. Choyamba, tikayeza zionetsero za kugwidwa ndi chiwanda mwa onena za kusogolo kapena wa matsenga, tiona kuti amanjenjemera mwakhunyu, kuwala ndiposo ngakhale kukomoka. Kenako malilime awo amasintha ndipo mawu osadziwika bwino amatuluka pakamwa pawo mosafuna. Iwo amalankhula m’malilime achilendo.
Azamatsenga onse ndi Akristu amene anagwidwa ndi ziwanda kudzera mu kuika manja ndiye eni ake a zochitika zimenezi. Pamene wachitsitsimutso wachikoka watenga maikolofoni yake ndi kufuula, “Ndi moto, ndi moto, ndi moto,” anthu osonkhana amasangalala ndipo amalephera kuzigwira. Anthu amene amafuna kuikidwa manja kwa iye amabwera kutsogolo. Iwo amakhala ndi manjenje osagwirika ndi kulankhula m’malilime. Zionetserozi ndi ntchito ya ziwanda zimene zikunamizira kuti zikugwira ntchito ya Mzimu Woyera. 
Anthu ogwidwa ndi mizimu yoipa, imene ingaitanidwe ndi wamaula ndi a zamatsenga dera lililonse la chipembezo chakale, amaonetsa zitsanzo zimodzi modzi ndi Akristu amene ndi ogwidwa ndi ziwanda kudzera mu kuika manja. Komabe, anthu samamvetsetsa ichi, ngakhale pali chitsimikizo chimenechi. Akristu amenewo ndi okankhidwa mu chisokonezo chakuya chifukwa iwo akuganiza kuti analandira Mzimu Woyera akakumana ndi zizindikiro zotere. 
 

Satana amagwira ntchito kudzera mwa Akristu ngati wamaula 

Satana amapangitsa anthu ogwidwa ndi ziwanda kuti apange mapemphero olosera. Iwo amanenera ponena kuti, “Iwe uzakhala mtsogoleri wabwino. Nkhosa zikwi zizadyera patsogolo pako. Mulungu azakuphunzitsa mtsogolo ndi kukupanga mtsogoleri wabwino kuchokera mwa iwe.” Kwa ena amalankhula mawu achenyengo monga, “Iwe udzakhala kapolo wapamwamba wa Mulungu. Udzakhala kapolo wa mkulu kwambiri wa Mulungu,” ndi cholinga chakuti alimbikitse anthu kuti awatsatire ndi kukhala monga akapolo a ziwanda moyo wao wonse. 
Amawula amaneneranso za tsogolo la anthu ena. “Muyenera kukhala tcheru ndi madzi mtsogolo.” “Mudzapanga ndalama zambiri.” “Mzimbambo wolemekezeka bwino azaonekera ku m’mawa ndi kukuthandiza iwe.” Izi ndi zitsanzo za zinthu zimene iwo amanena. Chizindikiro choyamba chimene chimaonekera mu anthu ogwidwa ndi ziwanda ndi chakuti iwo amanenera zabodza. 
Kenako iwo amalankhula m’malilime amene sangathe ndi kuzimvetsetsa okha. Iwo amanjenjemera ndipo amaonetsa ngakhale zizindikiro za kusokonezeka kwa khalidwe la umunthu. Ngati mwakumana ndi wamaula kapena wa matsenga, kodi munganene kuti iwo ali ndi khalidwe loyenera? Kawili kawili amalankhula mwa mwano kwa anthu amene ndi akulu kuposa iwo.
 Komabe, anthu amene ali ndi kukhazikika koona kwa Mzimu Woyera anamulandira Iye mwakukhulupilira mu choona cha m’baibulo chimene chimanena kuti Yesu anachotsa machimo onse a dziko kudzera mu ubatizo Wake ndi imfa pa Mtanda. Anthu awa amathandizanso ena kuti adziwe ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, ndi kuwathandiza kuti alandire chikhululukiro cha machimo ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Iwo okha amafuna kukhala mnjira ya chilungamo, ndipo makhalidwe awo ndi okondweretsa kwambiri ndiponso oyenera kutsogolera ena ku chikhulupiliro chodalitsika cha Mulungu ndi ku umoyo umene Mulungu amafuna. Pomwepo Mulungu amawadzudzula ndi cholinga chakuti awasunge angwiro ngati nzeru zawo zikafuna kubwerera ku dziko. 
Olungama amene analandira chikhululukiro cha machimo awo onse ndi osiyana mwathunthu ndi anthu amene umunthu wawo unaonongedwa ndi mizimu yoipa. Umunthu woona umabweranso kachiwiri ngati munthu walandira chikhululukiro cha machimo ndipo kenako walandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Mowonjezera, wolungama ali ndi nkhawa kwambiri za ena pansi nyengo zosakhala bwino, pa zimene iwo akufunika kweni kweni mu mawu a Mulungu, kuwapemphelera kuti aomboledwe, ndi kudzipereka iwo okha kuti awathandize iwo. 
Mbali ina, tingathe kuona kuti umunthu wa anthu ogwidwa ndi ziwanda unaonongedwa koopsa. Satana amawalamulira ndi kuwakhotetsera ku chifuniro chake chifukwa iwo amaganiza kuti zinthu ngati kunjenjemera ndi kulankhula m’malilime ndi mphatso za Mzimu Woyera. Komabe, zinthu zimenezi mosakaikira si mphatso za Mzimu Woyera. 
Pali atumiki ochuluka kwambiri amene ndi onyadira mphamvu zao monga kunenera m’dzina la Mulungu, kukwanitsa kuchita zozizwitsa zambiri ndi kulankhula m’malilime. Koma ngati adakali ndi tchimo mu mitima yawo, ndiye kuti mphamvu zao ndi umboni wabodza kuchoonadi chakuti ndiwogwidwa ndi ziwanda. Choncho, iwo sangapereke kukhazikika kwa Mzimu Woyera kwa ena, koma angapereke kukhazikika kwa ziwanda kokha. Komanso, chifukwa Satana ndi wachinyengo, chodabwitsa chimene iwo achita chimatha ntchito m’nthawi yochepa.
Pali kusiyana koonekeratu pakati pa ntchito ya Mzimu Woyera ndi ntchito ya chiwanda. Ngakhale kuti chingaoneke monga ntchito ya Mzimu Woyera siimapereka china chilichonse chodziwika bwino kapena mphatso zosangalatsa pachiyambi, pamene nthawi ikupita, mphamvu ya Mulungu imakula mosalekeza m’mitima ya olungama monga dzuwa lokutuluka m’mawa.
 

Akristu ogwidwa ndi ziwanda

Kodi n’ chifukwa chiani anthu Ochuluka kwambiri amagwidwa ndi ziwanda ngakhale kuti amafuna kulandira Mzimu Woyera?
Chifukkwa amalandira ziwanda kudzera mu kuika manja kwa aneneri onyenga

Modabwitsa, tingathe kuona okhulupilira ambiri mwa Yesu amene mathupi ndi miyoyo yawo yaonongeka chifukwa analandira ziwanda kudzera mwa kuika manja ndi aneneri onyenga. Anthu awa alibe naye ntchito Mulungu chifukwa chikhululupiro chawo sichigona mu mawu a Baibulo. Ali kugwiritsa ntchito mphamvu zawo osadziwa kuti ntchito zawo zikupangitsa anthu ambiri kuti akhale akapolo a Satana. Kodi n’chifukwa chiyani amagwira ntchito molimbika kwambiri pakuchita mphamvu zawo mu Chikristu? Chifukwa izo zochedwa mphamvu zawo zizasowa posachedwa ngati sazigwiritsira ntchito? Ichi ndiye chifukwa chimene amakhala otanganidwa kwambiri. 
Iwo amapitiriza kupemphera kosalekeza ndi kuyesera kuchita zizindikiro ndi zionetsero mu dzina la Yesu. Anthu amene amanena kuti, “Ndalandira mphatso yolalikira uthenga wabwino,” afunika kulalikira uthenga wabwino kosalekeza chifukwa ngati satero, chisangalalo chawo chachinyengo chimasowa posachedwa. Ngati anthuwa siamvera mphatso za ziwanda za zolankhula m’malilime, kuchilitsa kapena, uneneri, mkulankhula kwina, ngati iwo sakhulupirika ku zinchito za Satana, ndiye kuti Satana angawapangitse kuti adwale popanda chifukwa cheni cheni. Chili ngati wamaula kapena sing’anga madwala mosalekeza akakana ntchito monga kapolo wa Satana. Ichi ndicho chifukwa akufunika kugwiritsa ntchito mphatso zimene alandira kwa Satana modzipereka pakuwopa kuti angasiyidwe m’manzunzo pambuyo pomaliza mphamvu zawo. 
Ndinali kudziwa munthu wina amene anali wokhulupilira kwambiri mwa Yesu ndipo analikuoneka ngati anali ndi mphamvu zambiri zochokera kwa Mulungu. Iye anali kulimbikitsa anthu kuti alandire kudzadza kwa Mzimu Woyera ndipo anali kutsogolera misonkhano za chitsitsimutso m`mene anali kuchotsa ziwanda kudzera mu kuika manja, komanso kuchita zozizwitsa monga kulakhula m’malilime ndi kuchilitsa. Iye anakhala chinthu chochititsa chidwi ndi kupasidwa ulemu kupitira m’ntchito yake yodabwitsa. Zikwi zochuluka za okhulupilira zinamutsatira. Komabe, posachedwa anayamba kumukana Yesu ponena kuti, “Yesu Kristu ndi wolephera. Iye si Mwana wa Mulungu.” Anatembelera Yesu Kristu ndipo analakhulanso kuti iye yemwe anali Mulungu. Pothera pake iye anapha Yesu Kristu mu mtima mwake ndi m’mitima ya Akristu ambiri. 
Anthu ngati awa amakana uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu chifukwa Satana ndiye owatsogolera. Iwo amakhala ndi chikhulupiliro cholakwika kuchokera pa chiyambi chifukwa ali ndi maganizo onyenga kuti ali ndi mphamvu zimodzi modzi ngati Atumwi, zoonetsa zokwanitsa zao, kupangaitsa anthu kulankhula m’malilime ena ndi kuchotsa ziwanda kudzera mu kuika manja. Iwo ali ndi chikhulupiliro chokhwima kuti kukhazikika kwa Mzimu Woyera kwabwera pa iwo. 
Iwo amaphunzitsa anthu za njira zolandiliramo Mzimu Woyera, kuganiza kuti ndichotheka kumulandira Iye mwakupemphera mapemphero akulapa. Komabe, njira iyi yolandiliramo Mzimu Woyera siyolingana ndi mawu a Mulungu. Ngakhale zili chonchi, iwo amanena kuti ngati okhulupilira amalankhula m’malilime ndi kunenera, ndiye kuti ichi ndi chitsimikizo chakubwera kwa Mzimu Woyera pa iwo. Chifukwa anthu ambiri samvetsetsa moona kukhazikika kwa Mzimu Woyera, iwo amakhulupilira kuti angalandirenso Mzimu Woyera pakuphunzira ndi kutsatira ziphunzitso za aneneri onyenga. Umu ndiye m`mene Satana anakwanitsira kudzadza Akristu ndi mizimu ya ziwanda ndi kukhala ndi ulamuliro pa anthu amenewa. Njira zonsezi ndi misampha ya Satana. 
Anthu ochuluka anagwidwa ndi ziwanda kudzera mu ziphunzitso za aneneri onyenga. Okhulupilira wamba amakhala moyo wachipembezo wobwereza, koma anthu ogwidwa ndi ziwanda amagwiritsa ntchito mizimu zoipa ndipo amaoneka ngati amakhala moyo wa chipembedzo. Kodi ndi kuthekera kotani kumene iwo amaonetsera? Ali ndi kuthekera kochilitsa, kulankhula m’malilime ndi kutsogolera ena kuti alowedwe ndi ziwanda kudzera mu kuika manja. Tiyenera kudziwa kuti kuika manja ndi njira yopatsira chinthu kwa ena ndiponso kuti ufumu wa ziwanda wakuzidwa kwakukulu kudzera m’njira imeneyi. 
 

Mizimu yoipa imagwira ntchito kudzera mu dyera la munthu!

Satana amagwira ntchito mwa anthu monga Simoni wa m’ndime yaikulu. Anthu awa amanena kuti angalandire Mzimu Woyera kudzera mu kuika manja, osasamala za chikhulupiliro mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Masiku ano anthu ochuluka akunyengedwa ndi satana, ndipo akuyesa kulandira Mzimu Woyera kudzera m’mapemphero akulapa, kusala kudya, kudzipereka kapena kuika manja. Komabe, iwo amagwidwa ndi ziwanda ndi kukhala moyo wotembeleredwa. 
Tiyenera kukhala odziwa bwino kuti Chikristu cha masiku ano chimathandiza ziwanda kuti zigwire ntchito mu moyo wa aliyense kudzera mu njira iyi yotchedwa kuti ‘Kuikapo manja.’ Anthuwa amene ali ndi machitidwe ofanana ndi Simoni ndi aneneri onyenga pamaso pa Mulungu. Ngakhale okhulupilira mwa Yesu, angagwidwe ndi ziwanda ngati ali ndi tchimo m’mitima yawo. Anthuwa amatha kuchita zodabwitsa kudzera mu ntchito za mdierekezi. Satana amatsogolera anthu kuti alandire kuika kwa manja kwa akapolo ake n’cholinga chakuti athandizire iwo kugwidwa ndi ziwanda ndi kumanga ufumu wake padziko lonse. Masiku ano, mipingo ya [2]Kayendetsedwe ka Chipentekoste Chachikoka ndiyo imazindikiridwa mwalamulo kukhala zipembezo za Chikristu pa dziko lonse mwatsatane tsatane. 
 
2Chikristu cha Kumadzulo chinayamba kufota chifukwa cha kupata chuma cha akatundu ndi kugwiritsa ntchito kwambiri m’nthawi yomaliza ya theka la zaka za mu 20th sentiwale. Panthawi imodzimodzi, chifukwa cha ichi, Akristu ambiri amene anali kufunafuna njira kuti ayende ndi Yesu anali osakhutila ndi kuuma kwa mipingo yawo yakumbuyoko. Ena anali kuzunzika mwina ndi kusowekera, kapena kukula kwapang’onpang’ono kwa muuzimu, ndiponso ena anali okhumudwitsidwa mwakulephera kwawo kuti amasulire chikhulupiliro chawo mu chikondi chaokha ndi Yesu. 
Otchedwa Mayendetsedwe Achikoka Achipentekosite anaukitsidwa chifukwa cha mavutowa. Onse aja analowa mu kayendetsedweka anali kufuna kuona zodabwitsa ndi kuchita monga kulankhula m’malilime, kunenera, kuchita zodabwitsa ndi zozizwitsa, kufunitsitsa zinthu za tsiku la Pentekosite la kale. Mu chidwi chawo, mozipereka amazilowetsa okha ku zotchedwa kuti ulamuliro wa Mzimu Woyera, koma kulankhula motsindika ambiri a maphunzitso awo ndi zochita sizigwirizana ndi Baibulo. 
Mdziko loyamba kutukuka, mayendetsedwewa atukuka kwambiri mkati mwa zofuna zawo. Azitsogoleri awo akoka dziko loyamba kutukuka la Akristu ndi madalitso achuma ndi thanzi pamodzi ndi chidwi cha chipembezo. Kukhotetsa kwina kwa mayendetsedwe ngati Chipentekoste-chatsopano chimaulutsidwa ngakhalenso ngati kukugawana ziphunzitso zimodzimodzi ngati za Mayendetsedwe a Nthawi Yatsopano.
 
Dzikoli lilikudza kumapeto pang’ono pang’ono. Ngati tikufuna kubadwa mwatsopano m’masiku omaliza, tifunika kudziwa m’mene mdierekezi amagwirira ntchito ndi kuima molimba ku ziwembu zake. Tifunikanso kupulumutsidwa ku machimo athu mwa kamodzi kokha ndi kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera
pokhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Tifunika kubwerera ku choonadi ndi kudziwa kwangwiro m’mene Mzimu wa Mulungu umabwerera kwa ife. 
Monga m’mene Mulungu ananenera, “Anthu anga aonongeka chifukwa cha kusadziwa” (Hoseya 4:6), masiku ano ofuna funa choonadi ochuluka amaonongedwa, pamene mu umbuli wao, asocheletsedwa ndi anthu achikoka. Anthu amanena kuti ngakhale kuti yotchedwa mipingo Yachikoka ya Pentekoste inapangidwira mu chipululu, anthu akanasonkhana kumeneko. N’chifukwa chiani ichi chili choncho? Anthu achikoka amakuza mipingo yawo posokoneza ena ndi mphamvu zawo zoyerekezera, nkuwatsogorera kuti agwidwe ndi ziwanda kudzera mu kuwaika manja. Limodzi mwa luso lawo lapadera dera ndilakuti anthu akagwidwa ndi ziwanda kudzera mu kuwaika manja, amakhala ndi chidwi chokhala moyo wa chipembezo. 
Chizindikiro china chapadera cha anthu achikoka ndi chakuti iwo amapereka ndalama zazikulu ku mipingo yawo ndipo mopanda malire kukhala okhulupilira odzipereka. Ngakhale Akristu ambiri ali ndi chidwi pa kulalikira ndi mphamvu za ziwanda, koma chodziwikiratu amapita ku gahena osazindikira mapeto awo omwe. Anthuwa, amene amakhulupilira kwakukulu mphamvu ya mdierekezi monga chitsimikizo cha chipulumutso chawo, akuyembekezera kumwamba popanda ndi chikaiko chilichonse. Komabe, iwo ali ndi tchimo m’mitima yawo ndipo ndiwogamulidwa kuti akaonongedwe. 
Ngati afunsidwa funso lotsatirali, “Kodi uli ndi tchimo mu mtima mwako, ngakhale umakhulupilira mwa Mulungu?” Ndithudi iwo amayankha kuti ndi chachilengedwe kwa iwo kukhala mu uchimo. Iwo amaganiza kuti ndichosatheka kwa munthu kukhala opanda tchimo mu mtima mwake, ngakhale kuti amakhulupilira mwa Yesu. 
Anthu amakonda kuganiza kuti iwo ayenera kukhala mu ufumu wa Kumwamba, ngakhale kuti ali ndi tchimo m’mitima yawo, chifukwa amamva chitonthozo pokhulupilira mwa Yesu pokhala ndi chitsimikizo cha mphamvu-yabodza. 
Chiyembekezo chopanda pake motani chimenechi! Chifukwa cha chikhulupiliro chawo cholimba ndi chakuti iwo ali ndi luso lina lake lauzimu. Iwo analankhulapo m’malilime, kulandira masomphenya ndi kuchilitsa odwala, ndipo amaganiza ndi kukhulupilira molimba kuti zochitika zimenezi ndi ntchito ya Mzimu Woyera. Motero, iwo amadziuza okha kuti ndizodziwikiratu kuti iwo alandira chiombolo ndi Mzimu Woyera kudzera m’zochitika zimenezi. 
Chifukwa anthu awa ali ndi kudziwa kolakwika za mawu a chipulumutso, iwo alibe chilimbikitso m’chipulumutso chawo ngati palibe chochitika chilichonse chowoneka kwa iwo. Choncho, anthu awa amayesa molimba kupeza zitsimikizo zowoneka za chipulumutso ndipo patsogolo pake amagwiritsidwa ntchito ndi Satana mu ntchito yake. Chifukwa anthuwa akufuna kupeza mayankho a Mulungu kudzera m’mapemphero akulapa kapena kudzipereka nsembe kuposa kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, iwo pothera pake amalandira mizimu yoipa m’malo mwa Mzimu Woyera. 
Mdierekezi amaimba anthu mlandu powanong’oneza m’makutu mwawo, “Iwe wachimwa, kodi sunatero?” ndi kuwatengera kuti agwere mu kudzitsutsa-okha. Pali munthu amene ndimam’dziwa amene tsopano analandira chikhululukiro cha uchimo ndi Mzimu Woyera. Ichi ndi chinthu chimene chinamchitikira asanabadwe mwatsopano, pamene anali wokhulupilira wodzipereka koma wosasamala mwa Yesu. Munthuyu anakalankhula ngakhale m’malilime ndipo ankachita zodabwitsa zambiri. Ngakhale kuti iye anafuula ndi kupereka mapemphero akulapa usiku wonse, mosayanganira chikhulupiliro chimene anali nacho mwa Yesu, tchimo lomwe linali mu mtimwa mwake linapitiliza kumzunza iye. Apa ndiye pamene manong’o nong’o a Satana anayamba. “Iwe wachimwa, choncho ndi chabwino kuti ufe kuposa kukhala moyo.” Satana ankabwera pafupi pafupi kwa iye ndi kumuimba mlandu, kumuzunza ndi kumukumbutsa iye za machimo ake. Satana anamutengera mu kudzitsutsa-yekha ndi kudziweruza-yekha. Komabe, chimene iye ankachita ndi kungovomereza machimo ake mumtima mwake. Iye sanathe kudzimasula yekha ku milandu ya Satana mpakana anamvera ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma. 
Muyenera kudziwa kuti iwo amene sakhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu amakhala chakudya cha mdierekezi. Kodi muganiza kuti wina wake amene sanalandire chikhululukiro cha machimo ali ndi mphamvu yokana mdierekezi? Aliyense amene sanakakamire ku uthenga wabwino woona wa madzi ndi Mzimu azagwidwa ndi kuzunzidwa ndi Satana. Uthenga wabwino wa Mulungu wa madzi ndi Mzimu ndiwoyenera kwambiri pakuthamangitsa Satana. Choncho, wina aliyense amene amakhulupilira mwa Yesu ayenera kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, ndiponso kuulalikira ku anthu onse apadziko. Iwo amene amamvera zimenezi ayenera kulemekeza ndi kukhulupilira mu zimenezi.
 

Chisinsi cha kusayeruzika chikugwira kale ntchito m’dziko!

Dziko lonse tsopano ndilophimbidwa ndi zochitika za ziwanda. Ngati tikufuna kulalikira uthenga wabwino umene umatengera anthu kuti alandire Mzimu Woyera, tifunika kuchotsa kusamvetsetsa kwakukuru pa za kukhazikika kwa Mzimu Woyera. 
Choyamba tifunika kunena momveka bwino kuti ndi bodza kuti Mzimu Woyera umadza kudzera mu kuika manja. Tiyenera kuchitira umboni poyera kuti zochitika monga “kulankhula m’malilime ena pambuyo poikidwa manja, kumva chinthu china kutentha kudzera mu kulapa ndi kusala kudya, ndi kumvera uthenga ochokera kwa Yesu molunjika” ndi ntchito za mdierekezi. Kudzera mu chikhulupiliro chokha mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu m`mene anthu angapulumutsidwire ku chinyengo cha mdierekezi. Ndi mwachikhulupiliro chokha kuti tingapulumutsidwire ku machimo athu kudzera mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
 Tifunika kugonjetsa mdierekezi, “tate wa mabodza,” ndi uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Satana wamanga anthu onse pa dziko lonse ndi maunyolo odzitsutsa-okha, choncho tiyenera kubweza anthu awa kuchoonadi pakuwapangitsa kuzindikira kuti zowachitikira zawo ndi zowakhuza ndi chinyengo cha Satana. 
Masiku ano, anthu monga Simoni Msamariya, yemwe anafuna kugula Mzimu Woyera ndi ndalama, akutumikira mu mpingo. Ndi akhungu omwe akutsogolera akhungu. Iwo sangaonetse anthu njira ya kuchipuluutso changwiro chifukwa iwo sadziwa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, ndipo ali ndi tchimo m’mitima yawo. Choncho amapangitsa Satana kuti akhale m’mitima ya owatsatira pakukhala ndi magawo a mapemphero a usiku wonse, kupemphera mapemphero akulapa ndi kugwiritsa ntchito kuika manja. Anthuwa moonadi ndiwogwidwa ndi mdierekezi, ndipo ngati tikufuna kuti abwerere ku mawu a Mulungu, tikufunika kuwononga ntchito ya Satana pakuwapatsa nzeru zangwiro za uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Ngati anthu sadziwa za njira za Satana, sadzakhala ndi chisankho chilichonse koma kubvutika kopanda kuzithandiza. 
Monga m`mene ndanenera, kuchita zodabwitsa monga kulankhula m’malilime ndi kusindikiza uneneri pambuyo polandira kuika kwa manja zonsezi ndi machitidwe za mdierekezi. Mkulankhula kwina, mphamvu za anthu achikoka zimaonekera kudzera mu ntchito za mdierekezi. Tifunika kuwaphunzitsa. “Ndi Satana amene amagwira ntchito mwa inu ngati muli ndi tchimo mu mtima mwanu. Ngati mukuganiza kuti Mzimu Woyera uli mwa inu, ngakhale kuti muli ndi tchimo mu mtima mwanu, ndiye kuti mwanyengedwa.” 
Chikhulupiliro cha Atumwi ndi cha anthu amene analandira kuika kwa manja mundime yaikulu ya Machitidwe a Atumwi 8 chinaikidwa mgulu limodzi, chifukwa onse anali kudziwa za uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu wa Yesu Khristu. Koma chikhulupiliro cha Atumwi chinali chosiyaniranatu ku cha Akristu ambiri a masiku ano amene amakhulupilira kuti kuika manja kokha kumawapangitsa kuti alandire Mzimu Woyera. 
Kodi munthu amalandira Mzimu Woyera kudzera mu kuika manja ndi munthu amene analandira chikhululukiro cha machimo? Ai. Baibulo limanena kuti Mzimu wa Mulungu unali kufungatira pamwamba pa madzi (Genesis 1:2). Ichi chitanthauza kuti wina alandire chikhululukiro cha machimo ndi Mzimu Woyera, iye ayenera kumvera ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Mulungu amatuma Mzimu Woyera ngati mphatso kwa Mkristu obadwa-mwatsopano amene wakhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. 
Tiyenera kukhala nacho m’maganizo kuti chingakhale ngati kutsutsana ndi uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, umene Mulungu anafuna kutipulumutsiramo ku machimo athu, ngati tingaphunzitse anthu kuti adziikidwa manja kuti alandire Mzimu Woyera. Kuganiza kuti munthu angapatse wina Mzimu Woyera chili ngati kulimbana ndi Mulungu, ndipo amene ali ndi chikhulupiliro chotere amagwera m’misampha ya Satana posachedwa. Ichi sichiyenera kuloledwa kuchitika. 
Machimo athu onse amakhululukidwa tikakhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, ndipo Mzimu Woyera umachitira umboni za izi. Munthu amene amakhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu alibenso tchimo mu mtima mwake. Ichi sichifukwa chakuti sanachimwe, koma m’malo mwake iye amakhulupilira mu mphamvu ya uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu umachitira umboni kuti iye alibe tchimo mu mtima mwake, ndipo Mzimu Woyera umachitiranso umboni wa izo. Wina sangaitane Yesu Mpulumutsi wake popanda kukhala ndi Mzimu wa Mulungu mwa iye. 
Anthu ogwidwa ndi ziwanda sadziwa za uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, ndipo samaipanga kukhala nkhani yokambirana. Sadziwa ngakhale uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, komanso satha kuzindikira choona. Iwo amanena kuti Mzimu Woyera umabwera pokhapo akachita ndi kulandira kuika manja. Komabe, Mzimu Woyera subwera kudzera mu kuika manja. Muyenera kuzindikira kuti ntchito za mdierekezi tsopano zili ndi mphamvu yaikulu pa anthu m’mipingo padziko lonse ndi ziphunsitso zake zabodza. Pachifukwa chimenechi, n’chofunikira kulandira kukhazikika koona kwa Mzimu Woyera mwa kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.