(Macitidwe a Atumwi 19:1-3)“Ndipo panali, pamene Apolo anali ku Korinto, Paulo anapita pa maiko a pamtunda, nafika ku Efeso, napeza akuphunzira ena; ndipo anati kwa iwo, Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupira? Ndipo anati, Iai, sitinamva konse kuti Mzimu Woyera waperekedwa. Ndipo anati, Nanga mwabatizidwa m’ciani? Ndipo anati, mu ubatizo wa Yohane.”
Kodi n’chifukwa chiani Baibulo limenena kuti, “Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikra tsopano lino Ufumu wa Kumwamba uli wokangamizidwa, ndipo okangamirawo aukwatula ndi mphamvu?”
Chifukwa anthu angatenge Ufumu wa Kumwamba mwachikhulupiliro mu uthenga wabwino wokoma umene umanena kuti Yesu anachotsa machimo onse adziko kudzera mu ubatizo Wake ndi Yohane ndi mwazi Wake pa Mtanda.
Kodi ndi uthenga wabwino otani umene Paulo ankalalikira? Analalikira uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Macitidwe a Atumwi 19:1-2 akunena kuti, “Ndipo panali, pamene Apolo anali ku Korinto, Paulo anapita pa maiko a pamtunda, nafika ku Efeso, napeza akuphunzira ena; ndipo anati kwa iwo, Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupira?” Komabe, anthuwa ankakukhulupilira mwa Yesu koma anali kusiya tanthauzo la ubatizo wa Yesu. Iwo sankadziwa uthenga wabwino okoma umene umatengela kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Ndi chifukwa funso la Paulo lakuti, “Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupira?” linali funso lachilendo kwambiri kwa ophunzira ena ku Efeso. Anthu ena akanawafunsa kuti, “Kodi munakhulupilira mwa Yesu?” Koma Paulo anafunsa funso ili m’njira yodabwitsa choncho kuti alandire Mzimu Woyera pakukonzanso chikhulupiliro chawo mu uthenga wabwino wokoma. Utumiki wa Paulo unali kulalikira uthenga wabwino okoma wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Paulo, Petro ndi Yohane anachitiranso umboni ku ubatizo wa Yesu ndi Yohane Mbatizi.
Tiyeni tione umboni wa atumwi ku uthenga wabwino wa ubatizo. Poyamba Paulo anachitira umboni nati, “Msatero ai. Ife amene tiri akufa ku ucimo, tidzakhala bwanji cikhalire m’menemo? Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwa Kristu Yesu; tinabatizidwa mu imfa yace?” (Aroma 6:2-3) ndi “Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Kristu munabvala Kristu” (Agalatiya 3:27).
Mtumwi Petro nayenso anachitira umboni ku uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu mu 1 Petro 3:21-22, kunena kuti, “Cimenenso cifaniziro cace cikupulumutsani tsopano, ndico ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lace la thupi, komatu funso lace la chikumbu mtima cokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Kristu; amene akhala pa dzanja lamanja la Mulungu atalowa m’Mwamba; pali angelo ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zomgonjera.”
Mtumwi Yohane anachitranso umboni wa uthenga wabwino okomawu mu 1 Yohane 5:5-8. “Koma ndani iye wolilaka dziko lapansi, koma iye amene akhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu; Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, ndiye Yesu Kristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi. Ndipo Mzimu ndiye wakucita umboni, cifukwa Mzimu ndiye coonadi. Pakuti pali atatu akucita umboni, Mzimu, ndi madzi, ndi mwazi; ndipo iwo atatu ali mmodzi.”
Yohane Mbatizi anagwira ntchito yofunikira kwambiri yomalizitsa uthenga wabwino okoma. Baibulo limanena zotsatirazi za Yohane Mbatizi mu Malaki 3:1-3 ndi Mateyu 11:10-11. Yohane Mbatizi anali woimilira mtundu wa anthu ndipo anali Eliya onenedwa alinkudza, monga kunalembedwa mu Chipangano Chakale. M’chipangano Chakale, nsembe ya chimo inali kuphedwa kuti ikhetse mwazi wake pambuyo pochotsa machimo a munthu kudzera mu kuika manja ake. Koma, m’Chipangano Chatsopano, Yesu ndiye nsembe ya tchimo amene anachotsa machimo onse a dziko kudzera mu ubatizo Wake ndi kufa pa Mtanda kuti alipire mphoto ya uchimo. Yesu anapulumutsa mtundu wa anthu chifukwa Yohane Mbatizi anapereka machimo onse adziko kwa Iye kudzera mu ubatizo mu Mtsinje wa Yordano.
Mulungu anakonza mitundu iwiri ya machitidwe akulu akulu n’cholinga choti apulumutse mtundu wa anthu ku machimo awo ndipo Iye anakwaniritsa onse. Choyamba chinali kupangitsa Yesu kubwera m’dzikoli kudzera mthupi la namwali Mariya, ndi kumpangitsa kuti abatizidwe ndi kupachikidwa kuti achotse machimo onse dziko. Chachiwiri chinali kupangitsa Yohane Mbatizi kubadwa kudzera mwa Elizabeti. Mulungu anapangitsa zochitika ziwiri izi kuti zikhaleko n’cholinga choti apulumutse mtundu wa anthu ku machimo awo. Iyi inali ntchito yokonzedwa ndi Mulungu mu Utatu. Mulungu anatuma Yohane Mbatizi m’dzikoili miyezi isanu ndi umodzi Yesu asanabwere, kenako anatuma Yesu Kristu, Mpulumutsi wa mtundu wa anthu, m’dzikoli kuti amasule mtundu wa anthu ku chiweruzo cha machimo awo.
Yesu anachitira umboni Yohane Mbatizi mu Mateyu 11:9. “Koma munatururkiranji? Kukaona mneneri kodi? Indetu, ndinena kwa inu, wakuposa mneneri.” Moonjezera, pamene Yohane Mbatizi, amene anapereka machimo onse a dziko kwa Yesu, anamuona tsiku lotsatirapo, anachitira umboni kunena kuti, ““Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” (Yohane 1:29)
Baibulo ili ndi mbiri zochuluka za Yohane, amene anabatiza Yesu, ndipo tiyenera kulimbikira kuti tim’dziwe bwino iye. Yohane Mbatizi anabwera m’dziko lino Yesu asanabwere. Ntchito yake inali kukwaniritsa uthenga wabwino okoma, chimene chinali chikonzero cha Mulungu. Baibulo limanena kuti Yesu anabvomera machimo onse adziko kuchokera kwa Yohane ndiponso kuti Yohane anapereka kwa Iye kuti akwaniritse chifuniro cha Mulungu.
Timamutcha Yohane Mbatizi chifukwa anabatiza Yesu. Kodi ndi tanthauzo lotani limene ubatizo wa Yesu kwa Yohane lili nalo kweni kweni? Liwu loti “ubatizo” limatanthauza kutsukidwa.” Pakuti machimo onse adziko anaperekedwa kwa Yesu kudzera mu ubatizo Wake, onse anatsukidwa. Ubatizo wa Yesu unali ndi tanthauzo lofanana ndi “kuika manja” kumene nsembe ya tchimo inkalandira mu Chipangano Chakale. Tanthauzo lauzimu la ubatizo ndi “kupatsira,” “kutsukidwa” kapena “Kukwililidwa.” Ubatizo wa Yesu kwa Yohane Mbatizi unali mchitidwe wa chiombolo kuchotsa machimo onse m’dziko.
Ubatizo wa Yesu uli ndi tanthauzo lofanana ndi kuika manja, imene inali njira yopatsiramo machimo ku nsembe ya tchimo mu Chipangano Chakale. Mkulankhula kwina, anthu a Israeli anali kupereka machimo awo a pachaka pa nsembe ya uchimo pa Tsiku Lachitetezero cha machimo kudzera mu kuika manja kwa mkulu wa nsembe. Nsembeyi mu Chipangano Chakale inali ndi ntchito yofanana ndi ubatizo wa Yesu ndi imfa Yake pa Mtanda.
Mulungu anasankha Tisku Lachitetezero cha machimo ngati nthawi yochotsera machimo a Israeli. Pa tsiku la khumi la mwezi wa chisanu ndi iwiri, mkulu wansembe anali kupereka machimo onse a pachaka a anthu pa mutu wa nsembe ya uchimo mwakuika manja ake pa nsembeyo kuti atetezere machimo a anthu. Iyi inali ndondomeko yakaperekedwe ka nsembe imene Mulungu anapanga. Iyi inali njira yokhayo yoperekera machimo a anthu pa nsembe ya uchimo, ndipo kutumiza tchimoli kudzera mu kuika manja linali lamulo lamuyaya limene Mulungu anapanga.
“Ndipo Aroni aike manja ace onse awiri pamutu pa mbuzi yamoyo, ndi kubvomereza pa iyo mphulupulu zonse za ana a Israyeli, ndi zolakwa zao zonse, monga mwa zochimwa zao zonse; naike izi pamutu pa mbuziyo, ndi kuitumiza kucipululu ndi dzanja la munthu wompangiratu, ndi mbuziyo isenze yokha mphulupulu zonsezo kumka nazo ku dziko la palokha; ndipo azitaya mbuziyo m’cipululu ” (Levitiko 16:21-22).
Mu Chipangano Chakale, wochimwa anali kuika manja ake pamutu pa nsembe ya uchimo ndi kupereka machimo ake pa iyo kuti akhululukidwe. Ndipo pa Tsiku Lachitetezero cha Machimo, Aroni mkulu wansembe, pokhala woimilira wa Israyeli onse, ankaika manja ake pa mutu pa nsembe kuti apereke machimo a Israyeli. Kenako nsembeyo inali kuphedwa ikatenga machimo awo.
Chili ndi tanthauzo lofanana ndi ubatizo (Baptisma mu Chigiriki kutanthauza kuti “kutsukidwa, kukwililidwa, kupereka”) umene Yesu analandira kwa Yohane mu Chipangano Chatsopano . Monga m`mene wansembe wamkulu mu Chipangano Chakale ankaikira manja ake pa nsembe ya uchimo kuti apereke machimo a anthu a Israyeli, choncho machimo onse a anthu anaperekedwa kwa Yesu kudzera mu ubatizo Wake ndi Yohane Mbatizi. Kenako Yesu anafa pa Mtanda kuti atetezere machimo a athu. Uwu ndi uthenga wabwino wokoma wa choonadi.
Monga m`mene Aroni mkulu wansembe ankaperekera nsembe yotetezera machimo m’malo mwa anthu a Israyeli, Yohane Mbatizi, m’modzi mwa ana a Aroni, anagwira ntchito ngati woimilila mtundu wa anthu pobatiza Yesu, ndipo mwakutero anapereka machimo onse a anthuwa pa Iye. Mulungu anafotokoza chikonzero chodabwitsa cha chikondi Chake mu Baibulo motere mu Masalimo 50:4-5, “Kumwamba adzaitana za kumwamba, Ndi dziko lapansi, kuti aweruze anthu ace: Mundisonkhanitsire okondedwa anga; Amene anapangana ndi Ine ndi nsembe.” Ame, Aleluya.
Mbiri ya Mpingo inanena kuti kunalibe chikondwelero cha kubadwa kwa Yesu zaka mazana awiri oyamba mu mpingo woyamba. Akristu a mpingo woyamba pamodzi ndi Atumwi a Yesu anali kukumbukira chabe January 6th kukhala “Tsiku la Ubatizo wa Yesu” ndi Yohane Mbatizi pa mtsinje wa Yordano. Kodi n’chifukwa chiani iwo ankatsindika kwambiri pa ubatizo wa Yesu mzokhulupilira zawo? Yankho lake ndilo kiyi weni weni ku Chikristu cha chikhalidwe cha Atumwi. Koma ndiyembekezera kwa inu kuti musasokonezeke ndi ubatizo wa madzi wa okhulupilira ndi ubatizo wa Yesu.
Ubatizo wa okhulupilira m`mene ulili masiku ano uli ndi tanthauzo losiyana kwambiri ndi ubatizo umene Yesu analandira kwa Yohane Mbatizi. Choncho, tonse tiyenera kukhala ndi chikhulupiliro chimodzi monga ophunzira a Yesu ngati tifuna kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Tonse tiyenera kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera mwakukhulupilira mu ubatizo wa Yesu, umene analandira kwa Yohane, ndiponso mu mwazi Wake umene anakhetsa pa Mtanda.
Ngati mpingo woyamba unaganiza za ubatizo ngati mwambo waphindu kwambiri, chinali chifukwa cha chikhulupiliro chawo chofunikira mu ubatizo wa Yesu, ndipo masiku ano tiyenera kutenga ubatizo wa Yesu ngati chipangizo chofunikira kwambiri ku chipulumutso chathu. Moonjezera, tiyenera kukumana ndi kusunga chikhulupiliro choyenera cha nzeru yangwiro, chimene chimanena kuti Yesu anayenera kupachikidwa chifukwa cha ubatizo wake ndi Yohane. Tifunika kukhala nacho m’maganizo kuti Mzimu Woyera umayamba kukhala mwa ife tikakhulupilira kuti Yesu anabatizidwa, nafera pa Mtanda ndipo anaukitsidwa kuti akhale Mpulumutsi wathu. Ubatizo wa Yesu ndi Yohane ndi mwazi Wake pa Mtanda uli ndi tanthauzo lapadera mu uthenga wabwino okoma.
Njira yokhayo kwa ife kuti tilandiremo Mzimu Woyera ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi. Ubatizo wa Yesu unayeretsa machimo onse a munthu kamodzi kokha. Unali ubatizo wachiwombolo umene umatitengera ife kulandira Mzimu Woyera. Pakuti anthu ena sazindikira mphamvu ya ubatizo wa Yesu, iwo amaumvetsa kukhala mwambo chabe.
Ubatizo wa Yesu umapanga mbali ina ya uthenga wabwino okoma, umene umafotokoza m`mene Iye anachotsera machimo onse a dziko ndi kuvomera chiweruzo chake mwakukhetsa mwazi pa Mtanda. Wina aliyense amene amakhulupilira mu mau a uthenga wabwino okoma uwu amakhala m’modzi wa mpingo, umene uli chuma cha Ambuye, ndiponso amadyelera madalitso a Mzimu Woyera. Mzimu Woyera ndi mphatso yochokera kwa Mulungu kwa iwo amene anakhululukidwa machimo awo.
Ndi ubatizo Wake, Yesu anakhala “Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa tcimo lace la dziko lapansi” zili bwino (Yohane 1:29). Mu Yohane 1:6-7 akunena kuti, “Kunali munthu, wotumidwa ndi Mulungu, dzina lace ndiye Yohane. Iyeyu anadza mwa umboni kudzachita umboni za kuunikaku, kuti onse akakhulupirire mwa iye.” Kuti tikhulupilire mwa Yesu ngati Mpulumutsi wathu, amene anachotsa machimo athu onse, tiyenera kumvetsetsa utumiki wa Yohane ndi umboni m`mene kunalembedwera mu Baibulo. Kenako tizatha kukhulupilira mwa Yesu ngati Mpulumutsi wathu. Kuti tilandire Mzimu Woyera, tifunikanso chikhulupiliro chathu cholimba chokhwimitsidwa ndi umboni wake. Choncho, kuti tikwanilitse uthenga wabwino okoma wa choonadi, tiyenera kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi Yohane ndi m’mwazi Wake pa Mtanda.
Mu Mateyu 11:12 chinalembedwa kuti, “Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa Kumwamba uli wokangamizidwa, ndipo okangamirawo aukwatula ndi mphamvu.” Ndimeyi imadziwika kuti ndi imodzi mwa ndime zobvuta kwambiri mu Baibulo. Komabe, tiyenera kukhala tcheru ku mau oti “kuyambira masiku a Yohane Mbatizi.” Ndithudi akutchula kuti utumiki wa Yohane unali wolumikizana ndi utumiki wa Yesu ku chipulumutso chathu.
Yesu akufuna ife kuti tilowe ufumu wa Kumwamba mwachikhulupiliro cholimba, molimba ngati azibambo akhama. Timachimwa masiku onse, ndife osalimba, koma Iye amatilola kulowa mu Ufumu Wake pakuyesa chikhulupiliro cholimba nzeru za kuipa kwathu. Choncho ndimeyi imatanthauza kuti anthu angatenge ufumu wa kumwamba mwachikhulupiliro mu uthenga wabwino okoma umene umanena kuti Yesu anafufuta machimo onse adziko kudzera mu ubatizo Wake ndi Yohane ndi mwazi Wake pa Mtanda. Mkulankhula kwina, zikutanthauza kuti Mwamba ungatengedwe kudzera mwa chikhulupiliro cholimba mu uthenga wabwino okomawu wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi.
Ubatizo wa Yesu unachotsa machimo athu onse, ndipo chikhulupiliro chathu mwa iwo chilonjeza kuti tizalandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Tiyenera kulalika uthenga wabwino uwu kwa anansi athu, abale, abwenzi, ndi kwa wina aliyense mu dziko lapansi. Tiyenera kukhala ndi chikhulupiliro mu uthenga wabwino okoma umene umanena kuti machimo a dziko anaperekedwa pa Yesu kudzera mu ubatizo Wake. Kudzera mu chikhulupiliro chathu tidzakhala ndi chisangalalo cha chiwombolo ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera.
Ubatizo wa Yesu unachotsa machimo athu onse, ndipo mwazi Wake ndiwo unali chiweruzo cha uchimo. Tifunikira kumasulira uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu kwa osakhulupilira. Ndipochita choncho, pamene adzakhulupilira mu uthenga wabwino ndi kulandira Mzimu Woyera. Ndifuna kuti inu mukhulupilire uwo. Ndi pakukhala ndi chikhulupiliro mwa ubatizo wa Yesu ndi Yohane ndi mwazi Wake pa Mtanda ndi pamene munthu angakhululukidwe ku machimo ake onse ndi kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera.
Aliyense angakhale mwana wa Ambuye, momwe Mzimu Woyera umakhala, ndiponso m’modzi wa abale ndi alongo athu mwakukhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. Muyenera kukhala ndi chikhulupiliro chofanana mu uthenga wabwino okoma ngati chimene Paulo anali nacho. Ndikuthokoza ndi kuyamika Ambuye pakutipatsa uthenga wabwino okomawu. Ame.