• All e-books and audiobooks on The New Life Mission website are free
  • Explore multilingual sermons in global languages
  • Two new revised editions in English have been released
  • Check out our website translated into 27 languages
Search

Sermons

Mutu 8: Mzimu woyera

[8-4] Iwo Amene ali ndi Chikhulupiliro Chofanana Monga cha Ophunzira a Yesu (Macitidwe a Atumwi 3:19)

Iwo Amene ali ndi Chikhulupiliro Chofanana Monga cha Ophunzira a Yesu(Macitidwe a Atumwi 3:19)
“Cifukwa cace lapani, bwererani kuti afafanizidwe macimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zocokera ku nkhope ya Ambuye.”
 

Kodi atumwi anali ndi chikhulupiliro chotani?
Ankakhulupilira zonse mu ubatizo wa Yesu ndiponso mwazi Wake wa pa Mtanda.

Tikaona pa ophunzira a Yesu Kristu, kukula kwa chikhulupiliro chawo pamene anali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera kunali kosiyana moonekeratu ndi chikhulupiliro chawo pamene analibe. Thupi lawo silinkaoneka kusintha kulikonse, koma pamene analandira Mzimu Woyera, miyoyo yawo inasintha kotheratu ndi kuwala kwa Yesu Kristu. 
Boma limene ndimakhala lili ndi mapiri komanso nyanja zokongola. Pomwe Ndinali kuona malo abwino choterewa, ndinakhala okhutira ndi kudabwitsika kuti sindingathe koma kuyamikira Ambuye chifukwa cha chilengedwe chotere. Kaonekedwe ka madzi-owala kakung’animira kwa dzuwa kamapangitsa mtima wanga kukhutira ndipo dziko lilipafupi ndi ine kuoneka ngati golide. 
Koma pali malo ena kumene kukongola kotere sikumazionetsa kokha. Kuli malo kumene thambo ndi lonyezimira bwino, koma madzi pansi pa kuwala kwadzuwa akuoneka ngati chithaphwi. Kulibe kuwala kwa kaonekedwe kotero. Kuona Nyanja motere, ndimakuyamika Ambuye chifukwa cha uthenga wabwino okoma umene unayeretsa machimo anga ndi kundipezera ine kukhazikika kwa Mzimu Woyera. 
Popeza pamwamba pa Nyanja ya chithaphwi sipamatha kunyezimira, choncho tingakhalenso chitsekerezo cha kuwala kwa Mulungu ndipo mosadziwa tingaziyandikira ku malo osadziwika bwino chifukwa cha mkhalidwe wathu wa uchimo. Koma ngati Mzimu Woyera ukukhala mu mitima yathu, tizaoneka ngati ana a Mulungu ndi kutsogoleredwa kuti tilalikire uthenga wabwino kwa anthu ena. Chifukwa tinalola kuwala Kwake, tidzawala ngati kuunika. 
Chimodzimodzi, pamene Yesu anaukitsidwa, ophunzira Ake analandira Mzimu Woyera ndipo anakhala ana komanso atumwi a kuwala. Kuwala kwa Mzimu Woyera ndi dalitso lalikulu kwa onse ndipo motero anthu ambiri amafuna kulandira Mzimu Woyera. 
 
 

Chikhulupiliro cha mtumwi Paulo 


Kodi Paulo anali ndi chikhulupiliro chotani? Paulo, mukubvomereza kwake kwa chikhulupiliro, ananena kuti anali ophunzira ndipo nthawi zonse anali kuphunzitsidwa ndi Gamaliyeli, m’modzi wa aphunzitsi aakulu lamulo pa nthawi imeneyo, anatsatira chilamulo cha atate wake. Koma anaulula kuti ngakhale ndi lamulo, sakanapulumutsidwa ku machimo ake ndiponso anali, zoona zake, yemwe anapachika Yesu, Mpulumutsi wathu. Tsiku lina anakumana ndi Yesu pa njira ya ku Damasiko ndipo anakhala mlaliki wa uthenga Wake wabwino. Anali ndi chikhulupiliro mwa Yesu Kristu ngati Mwana wa Mulungu, amene anabwera m’dzikoli, anabatizidwa ndi Yohane kuti achotse machimo onse adziko, ndi kukhetsa mwazi pa Mtanda kuti anyamule chiweruzo chonse cha machimo amenewo. M’mawu ena, Paulo mu mtima wake anali ndi chikhulupiliro mu chikhululukiro cha uchimo. 
Ophunzira a Yesu anakhulupilira kuti ubatizo wa Yesu ndi Yohane ndi mwazi Wake pa Mtanda kunali kuwakhululukira machimo awo onse. Paulo anagawana chikhulupiliro chimodzi ndi ophunzira ndipo motero anapulumutsidwa ku machimo ake onse. 
Paulo anati mu Agalatiya 3:27, “Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Kristu mudabvala Kristu,” ndi kuulula chikhulupiliro chake mu ubatizo wa Yesu ngati chipulumutso chake. Ndiponso, Petro anati mu 1 Petro 3:21, “Cimenenso cifaniziro cace cikupulumutsani tsopano, ndico ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lace la thupi, komanso funso lace la cikumbu mtima cokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Kristu,” ndipo anaonetsa uthenga wabwino okoma kudzera mu ndimeyi. Ophunzira a Yesu anakhulupilira kuti ubatizo Wake ndi Yohane unayeretsa machimo onse a dziko. Anakhululukidwa ku machimo awo, ndipo sanalinso pansi pa tembelero la chilamulo mwa kukhulupilira mu choonadi chimenechi. 
Anakhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda. Pali umboni wakuti chikhulupiliro chimenechi chinali chofunika kuti akwaniritse kukhala ophunzira. Mu Macitidwe a Atumwi 1:21-22, akunena kuti, “Kotero kuyenera kuti wina wa amunawo anatsatana nafe nthawi yonseyi Ambuye Yesu analowa naturuka mwa ife, kuyambira ubatizo wa Yohane, kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba kutisiya ife, mmodzi wa awa akhale mboni ya kuuka kwace pamodzi ndi ife.” Kukhala ophunzira wa Yesu kumayamba ndi kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi Yohane. 
Choonadi chimene tikufuna kuti tikhululukidwe machimo athu ndi chikhulupiliro mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda. “Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Kristu mudabvala Kristu.” (Agalatiya 3:27). Motero, Paulo nayenso anakhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi Yohane komanso mu mwazi Wake wa pa Mtanda. 
Tiyeni tione mu Tito 3:5. “Zosati zocokera m’nchito za m’cilungamo, zimene tidacita ife, komatu monga mwa cifundo cace anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera.” Apa ndemanga yakuti, “kutsuka kwa kubadwanso” kukutanthauza kuti machimo onse a dziko lapansi anayeretsedwa pamene Yohane anabatiza Yesu. Chimodzimodzi, ngati mukufuna kuti mukhululukidwe machimo anu, ndiyeno mukufunika kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma, umene umanena kuti machimo anu anaperekedwa kwa Yesu kudzera mu ubatizo Wake ndi Yohane. Chifukwa chimene Yesu anapachikidwira ndi kukhetse mwazi mpaka kufa chinali chakuti anachotsa machimo athu onse kudzera mu ubatizo umene analandira kwa Yohane. Kukhulupilira mu choonadi chimenechi ndi kokwanira kuti mupeze kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Paulo anaulula kuti iyenso anali kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi Yohane ndiponso mu mwazi Wake wa pa Mtanda. 
Tiyeni tione mu Ahebri 10:21-22, inena kuti, “Ndipo popeza tiri naye wansembe wankuru wosunga nyumba ya Mulungu; tiyandikire ndi mtima woona, m’cikhulupiriro cokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuicotsera cikumbu mtima coipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera.” Apa, “osambitsidwa ndi madzi oyera” zikusonyeza ubatizo wa Yesu ndi Yohane, umene unayeretsa machimo onse a mtundu wa munthu. 
Motero, mu zonse Chipangano Chakale ndi Chipangano Chatsopano, tingapeze kuti chinthu chofunika kwambiri cha uthenga wabwino okoma ndi ubatizo wake ndi imfa Yake ya pa Mtanda. Inunso, muyenera kugawana chikhulupiliro chomwechi ngati cha Paulo. 
Masiku ano, Akristu ambiri amakhulupilira mwa Iye pachabe popanda kudziwa kuti pamene Yohane anabatiza Yesu, machimo onse adziko anatsukidwa. Azaumulungu ena amatsutsa kuti anthu ayenera kubatizidwa m’madzi kuti akhululukidwe machimo awo. Nkhani yotere ikupangidwa mwina chifukwa cha kusadziwa uthenga wabwino oonadi komanso okoma wa madzi ndi Mzimu, monga kunalembedwa mu Baibulo. Machimo athu sangakhululukidwe mu mwambo wamba pamene tabatizidwa m’madzi. Chikhulupiliro mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake chimatiyeretsa tonse ku machimo athu onse. Okhawo amene akhulupilira mu uthenga wabwino okoma ndi amene akhululukidwa ku machimo awo. Ndipo mwa pokhulupilira m’mwazi Wake , analipira chiweruzo chawo chonse. Okhawo amene ali ndi chikhulupiliro chotere ndi amene angalandire Mzimu Woyera. 
“Tiyandikire ndi mtima woona, m’cikhulupiriro cokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuicotsera cikumbu mtima coipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera” (Ahebri 10:22). Wolemba Ahebri akutiuza kuti tiyandikire pafupi ndi Mulungu ndi mtima woona m’chikhulupiliro chokwanira. Inunso muyenera kuyandikira kwa Iye ndi mtima woona mu chikhulupiliro chokwanira mu uthenga wabwino okoma. 
Masiku ano, Akristu ali ndi chiyembekezo chonse chopeza kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Koma Mzimu Woyera umakhala mwa okhawo amene machimo awo anakhululukidwa. Ambiri sadziwa chimenechi ndipo motero akufuna kulandira Mzimu Woyera popanda kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Iwo amene amakhulupilira mwa Yesu koma sakhulupilira mu ubatizo Wake ndi mwazi wa pa Mtanda sangalandire Mzimu Woyera. Chifukwa ndi chakuti alibe mtima woyera. 
Paulo anakhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda ndipo motero analandira Mzimu Woyera. Kuonjezerapo, anafalitsa chikhulupiliro chimenechi ndipo anazunzidwa chifukwa chokhala wampatuko. Koma chifukwa Mzimu Woyera unali mu mtima mwake, anakwanitsa kufalitsa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu kufikira mapeto ake. “Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.” (Afilipi 4:13). Tikuthokoza kukhazikika kwa Mzimu Woyera, iye anatumikira Mulungu ndi kukhala motetezedwa ndi Mzimu Woyera kufikira pamene anapita kwa Mulungu. Okhawo amene ali ndi chikhulupiliro monga cha Paulo ndi amene angalandire Mzimu Woyera. 
Tiyeni tione pa chikhulupiliro cha Paulo. Mu Akolose 2:12, akunena kuti, “Popeza munaikidwa m’manda pamodzi ndi Iye muubatizo, momwemonso munaukitsidwa pamodzi ndi Iye m’cikhulupiriro ca macitidwe a Mulungu, amene anamuukitsa Iye kwa akufa.” Iye anakhululukidwa ku machimo ake onse pokhulupilira mwa Yesu, amene anabatizidwa ndi Yohane. 
 
 

Kodi Chikristu chasintha motani kuyambira nthawi zakale? 


Tsopano tiyeni tione kuvomereza kwa mlongo amene anakhala ophunzira atalandira Mzimu Woyera mwa Yesu Kristu. 
“Ndinali kukalamba koma ndinalephera kubereka mwana, choncho kuti ndilandire madalitso Ake kudzera mu pemphero ndinapita ku mpingo uwu ndi uwo. Ngakhale pamene ndinali ndekha ku nyumba, ndinali kupemphera kufuna mwana pafupifupi ola limodzi kapena awiri ndipo kusintha zipembezo kumeneko kunakhala mbali ya moyo wanga wa masiku onse. 
Pamene Ndinali kukhala ndi umoyo wachipembezo umenewu pa ine ndekha, ndinakumana ndi munthu wachikulire. Iye anandiuza kuti ngati ndikufuna kupempha mwana kwa Mulungu, ndiyenera kulandira pemphero la kuika manja kuchokera kwa iye. Ndinamverapo kwina kuti mkazi ameneyu ndi mthenga wa Mulungu ndipo motero ndinamulola kuti aike manja ake pamutu panga. Panthawi imeneyo, ndinamvera zinthu zimene sindinazimverepo kale lomwe. Lilime langa linayamba kuzungulira, ndipo ndinali kulankhula m’zinenero zosiyanasiyana ndipo ndinamvera mphamvu yachilendo komanso yotentha ikundikokera pamwamba. 
Ndinatenga zochitika zimenezi kuona ngati ndinalandira Mzimu Woyera ndipo linali yankho Lake ku mapemphero anga. Mkazi amene anaika manja ake pa mutu panga ankaoneka ngati anali ndi mphatso ya Mzimu Woyera ndipo ankatha kunenera ndi kuchiritsa. Iye sanalandirepo maphunziro a mawu a Mulungu, koma kugwiritsira ntchito mphamvu za Mzimu Woyera, anathandiza abusa ambiri ndipo ophunzira analandira Mzimu Woyera kudzera mu kuika manja. 
Kuyambira pamenepo, ndinayamba kupezeka pa misonkhano yotere, umodzi umene unali kutchedwa kuti “[3]Kayendetsedwe ka Kukonzanso/chitsitsimutso.” Panthawi ya amodzi mwa mapemphero anga pa msonkhano umenewu, ndinamva kunjenjemera thupi langa lonse ndipo mtima wanga unatentha ndi chikondi cha Mulungu ndi anzanga oyandikana nawo. Chinthu chimodzi chimwechi chinachitikanso kwa ena ndipo anthu anali kukomoka ndi kumayankhula m’malilime. Kunali anthu amene anali ndi ziwanda kumeneko, ndipo mtsogoleri wa msonkhano umenewu anali kutulutsa ziwanda. Cholinga cha Kayendetsedwe ka kukonzanso/chitsitsimutso chinali kuthandiza anthu kuti amvere Mzimu Woyera kudzera mu zinthu monga kunjenjemera, kunenera, kutulutsa ziwanda, ndiponso kulankhula m’malilime. Koma mosasamala kanthu zinthu zonse, ndinali ndidakali ndi uchimo, ndipo machimo mu mtima mwanga ankandipangitsa kumva mantha ndi manyazi. 
 
3Kusandutsidwa koona ndi kwachibadwa ndipo ndi mbali yofunika pa umoyo wa Chikristu, ndipo kumabweretsa kukula kuuzimu, kuchitidwa umboni ndi chipatso cha Mzimu. Koma m’zaka za posachedwapa, kayendetsedwe kena katembenuza tanthauzo la “kusandutsidwa” mwa njira yakuti sizikubala chiringanizo chilichonse cha kukula kuuzimu m’mene anakufotokozera mu Malemba. “Kusandutsidwa” kwawo kumene kumatulutsa zinthu zosaweruzika, kunalembedwa ndi chikhalidwe chonse chimene chinanenedwa, ndipo kuli pamodzi ndi ziphunzitso zaumulungu-zoonjezereka kapena zosakhala za m’Baibulo komanso zimene akuchita. 
Izi ndi zina za ziphunzitso za mavuto ndiponso zochita zimene zinali kuthandizidwa mkati mwa kusandutsidwa kwa mkangano ndiponso kayendetsedwe ka chitsitsimutso: kutsindika kwakukulu pa chidziwitso cha achikoka pa Malemba, maonetseredwe abodza, ziphunzitso zabodza, uneneri wabodza, zizindikiro zabodza ndiponso zodabwitsa, ndi zina zotere. Komabe, chinthu choopsa kwambiri cha kayendetesedwe kameneka ndi chakuti achititsa anthu ambiri kusamvetsetsa choonadi cha kulandira Mzimu Oyera ndi kuika pambali uthenga wabwino okoma. 
 
Motero, nthawi zonse pamene Ndikupemphera, Ndimapemphera mozipereka kuti ndikwanitse kuthetsa mavuto a uchimo. Ndinaulula kuti ndinali ndi uchimo, koma anthu ankandionabe ngati m’ngelo. Ndinaganiza kuti ndinali ndi chikhulupiliro chabwino, koma ndinali kulakwitsa. Ndikanakhala kuti sindinathe kuzindikira kulakwitsa kwanga, sindinakakhala ndi mpata wolandira Mzimu Woyera. 
Kuchoka apo, ndinakumana ndi iwo amene amafalitsa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndipo ndinalandira chikhululukiro cha machimo anga onse pokhulupilira mu mawu a Mulungu. Tsopano ndinedi okondwera. Ndimakhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndipo ndinalandira Mzimu Woyera. Ndikuthokoza Mulungu. Ndikadakonda kuti Akristu onse padziko lonse lapansi akhulupilire mu uthenga wabwino okoma ndi kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Ndikuthokoza Ambuye wathu.”
Apa tinaphunzira kuti pofuna kuti tilandire Mzimu Woyera, tikufunika uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Ngati mukufuna kukhululukidwa machimo anu onse, muyenera kukhala ndi chikhulupiliro mu ubatizo wa Yesu ndi Yohane. Tiyeni tione mu Aefeso 4:5. “Ambuye mmodzi, cikhulupiriro cimodzi, ubatizo umodzi.” Apa akunena kuti pali Ambuye amodzi ndi ubatizo umodzi okha, umene tikhulupilira. Tiyenera tonse kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi Yohane ndiponso mwazi Wake wa pa Mtanda kuti tilandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Ngati sitichita choncho, ndiye kuti Mzimu Woyera suzakhala mwa ife. 
Nthawi ina kunali anthu amene anali kuphunzitsa ndi kukhulupilira kuti kuyeretsedwa ndi chiyeretso cha Kayendetsedwe kuzathandiza iwo kulandira Mzimu Woyera. Komabe, kodi muganiza kuti Mzimu Woyera ungakhale mwa ife ngati talumikizana ndi mayendetsedwe amenewa? Kodi munalandira Mzimu Woyera chifukwa cha kuyeretsedwa ndi chiyeretso cha Kayendetsedwe? Ngati zinali zotheka, ndiye kuti mukanakhala a nzeru kusunga chikhulupiliro chanu. Koma ngati Mzimu Woyera unabwera mwa inu pachifukwa ichi, ndiye kuti Yesu sakanayenera kubwera ndi kudzatipulumutsa kumachimo athu ndipo sakanayenera kubatizidwa ndi Yohane kapena kupachikidwa pa Mtanda. 
Kulandira kwa kukhazikika kwa Mzimu Woyera ndi mphatso yochokera ku chikhulupiliro cha mu uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, umene anabweretsa chikhululukiro cha machimo anu. Kukhazikika kwa Mzimu Woyera ndi mphatso inaperekedwa kwa iwo amene machimo awo anayeretsedwa ndi kukhululukidwa kudzera mu uthenga wabwino oona. 
Masiku ano, mwa iwo amene akuzipereka mu Kayendetsedwe ka kukonzanso/chitsitsimutso, pali ena amene amakhulupilira kuti mapemphero okweza a kulapa angawathandize kulandira Mzimu Woyera. Amanena kuti ngakhale kuti munthu ali ndi uchimo mu mtima wake, ngati angapemphere mapemphero akulapa, ndiye kuti adzalandira Mzimu Woyera. 
Kayendetsedwe ka chikoka cha Pentekoste, kamene kafalitsidwa padziko lonse lapansi, kanayambira ku United States mu ma 1800. Kayendetsedwe kameneka kanabwera pambuyo pa kukonzanso kwa zachuma, Pamene chikhalidwe ndi miyambo ya anthu zinatha. Kayendetsedwe kameneka kanafika pa tsiku lake lenileni pamene mitima ya anthu inali yopasulidwa chifukwa cha kukhumudwa kwambiri. Kuyambira nthawi imeneyo, chikhulupiliro chochokera mu mawu a Mulungu chinatha ndipo Kayendetsedwe katsopano kachipembezo kanayamba kukula. Kanali Kayendetsedwe kachikoka ka chipentekosite kamene kanali ndi cholinga cha kumvera Mzimu Woyera (Mulungu) mwakuthupi – kuona ntchito za Mulungu ndi maso ndi kumvera mphamvu za mawu a Mulungu ndi thupi ndiponso maganizo. 
Koma cholakwika choopsa mu kayendetsedwe kameneka ndi chakuti chimachotsa okhulupilira ku mawu a Mulungu ndi kukhazikika ngati chipembezo chimene chimavutikira madalitso athupi. Chifukwa cha chimenechi, otsatira a kayendetsedwe katsopano anakhala akuthandizira chi Shamanizimu. Ngakhale lero, iwo amene amazipereka okha mu Kayendetsedwe ka chikoka cha Chipentekosite amakhulupilira kuti, ngati munthu ali ndi chikhulupiliro mwa Yesu adzakhala wachuma, kudwala kwake kuzachiritsidwa, azakhala ochita bwino mu zonse, adzalandira Mzimu Woyera ndi kulankhula m’malilime ndi kukhala ndi mphamvu ya kuchiritsa ena. Kayendetsedwe ka chikoka cha Chipentekosite kafalitsidwa padziko lonse lapansi. Kayendetsedwe kameneka kakhala chitsekerezo ku chikhulupiliro cha anthu mu uthenga wabwino okoma ndi kuthekera kwawo koti apeze kukhazikika kwa Mzimu Woyera. 
Akristu a masiku ano anachokera mu zikhulupiliro za Luther ndi Calvin zaka pafupifupi 500 zapitazo. Koma mkati mwa malire a Chikristu, kuphunzira kwa Baibulo za kukhazikika kwa Mzimu Woyera sikunakhazikitsidwe molimba bwino. Vuto ndi lakuti kuyambira pachiyambi cha Chikristu cha masiku ano, Akristu ambiri akhulupilira mwa Yesu popanda kuzindikira tanthauzo la ubatizo Wake ndi imfa ya pa Mtanda. Kupanga zinthu kukhaliratu zoipa, anthu anayamba kukhulupilira mu chiphunzitso cholakwika cha Chikristu ndi kutsindika zochitika zathupi zokha. Akristu onse ayenera kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma umene umanena kuti Yesu anabatizidwa ndi Yohane kuti achotse machimo onse adziko lapansi ndiponso kuti anapachikidwa kuti aweruzidwe chifukwa cha machimo amenewo. Chikhulupiliro chimenechi chidzapangitsa kuti inu mulandire Mzimu Woyera. 
Masiku ano, chifukwa chimene Chikristu chakhalira chotayika ndi chakuti anthu ayamba kukana choonadi cha ubatizo wa Yesu analandira kwa Yohane ndiponso mwazi Wake wa pa Mtanda. Yesu amatiuza ife kuti tidziwe choonadi. Kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi Yohane ndiponso mwazi Wake wa pa Mtanda kukutanthauza kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Ngati mukufuna kulandira Mzimu Woyera, ndiyeno khulupilirani kuti pamene Yohane anabatiza Yesu, machimo anu anaperekedwa kwa Iye ndiponso kuti mwazi Wake unali chiweruzo ndiponso chikhululukiro cha machimo anu onse. Ndiyeno mudzalandira Mzimu Woyera. 
Akristu ambiri amakhulupilira mu mwazi okha wa Yesu ngati uthenga wabwino wachiombolo. Koma kodi iwo a inu amene mumakhulupilira mu mwazi Wake okha mungamasuke ku uchimo? Kodi mungatero? Ngati mukuganiza kuti ichi chingakhale tero, mwina muli ndi kudziwa kosaoneka bwino za tanthauzo loona la ubatizo wa Yesu. Ngati ndi choncho mudakali uchimo mu mtima mwanu. Pokhapo pamene mwalumikiza ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pamodzi ngati chikhulupiliro chimodzi ndi pamene mungapulumutsidwe kumachimo anu ndi kulandira Mzimu Woyera. Baibulo limanena kuti uwu ndi uthenga wabwino oona okhawo umene umathandiza inu kugonjetsa dziko. “Pakuti pali atatu akucita umboni, Mzimu, ndi madzi, ndi mwazi; ndipo iwo atatu ali mmodzi.” (1 Yohane 5:8). Motero, tiyenera kudziwa kuti, mu chifuniro Chake kuti atipulumutse kumachimo athu, Mulungu analola Yohane kumubatiza Yesu ndipo kenako kumupachika Iye. 
Chifukwa chimene Akristu ambiri alibe chikhululukiro cha machimo ngakhale amakhulupilira mwa Yesu ndi chakuti sakhulupilira mu uthenga wabwino okoma umene unakwaniritsidwa ndi ubatizo wa Yesu ndi Yohane ndiponso mwazi Wake wa pa Mtanda. Iwo amene amakhulupilira mu zinthu ziwiri izi adzakhululukidwa machimo awo ndipo Mzimu Woyera udzakhala m’mitima yawo. 
Pamene anthu azindikira kuti machimo awo ayeretsedwa, mitima yawo imakhala mu mtendere ndiponso yodzala ngati madzi odekha. Panthawi imene Mzimu Woyera wakhala mu mtima mwa munthu, mtendere ngati mtsinje umayenda mkati ndi kunja mwa mtima wake. Timakumana ndi Ambuye wathu mwa kukhulupilira mu choonadi chimenechi ndi kuyenda ndi Mzimu pamene tikufalitsa uthenga wabwino wa kulandira Mzimu Woyera. Mitima yathu sinakhalepo ndi mtendere otere. Kuyambira nthawi imene tinayamba kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, miyoyo yathu inakhala pamtendere ndipo mitima yathu inakhala yachimwemwe bwinobwino. Sitingabwerere kuchoka ku uthenga wabwino okoma umenewu. Mzimu Woyera nthawi zonse uli mu mitima yathu, ukutifulumizitsa kuti tifalitse mawu Ake ndi kulola anthu amene akhulupilira mwa iwo kuti alandire Mzimu Woyera. 
Chifukwa tinakhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda, tinadalitsidwa ndi Mzimu Woyera. Tsopano muyenera kukhala ndi chikhulupiliro mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda kuti mulandire Mzimu Woyera. Ndi kofunikira kuti anthu padziko lonse lapansi ayambe kufunafuna za kukhulupilira mu mawu a Mulungu kuti Yesu anabatizidwa ndi Yohane kuti achotse machimo onse adziko lapansi ndiponso kuti anafa pa Mtanda kuti aweruzidwe chifukwa cha machimo awo. Pamene achita choncho, Pomaliza adzalandira Mzimu Woyera.