(1 Yohane 1:1-10)“Cimene cinaliko kuyambira paciyambi, cimene tidacimva, cimene tidaciona m’maso mwathu, cimene tidacipenyerera, ndipo manja athu adacigwira ca Mau a moyo, (ndipo moyowo unaonekera, ndipo tidaona, ndipo ticita umboni, ndipo tikulalikirani moyo wosathawo, umene unali kwa Atate, nuonekera kwa ife); cimene tidaciona, ndipo tidacimva, tikulalikirani inunso, kuti inunso mukayanjane pamodzi ndi ife; ndipo ciyanjano cathu cirinso ndi Atate, ndipo ndi Mwana wace Yesu Kristu; ndipo izi tilemba ife, kuti cimwemwe cathu cikwaniridwe. Ndipo uwu ndi uthenga tidaumva kwa Iye, ndipo tiulalikira kwa inu, kuti Mulungu ndiye kuunika, ndipo mwa Iye monse mulibe mdima. Tikati kuti tiyanjana ndi Iye, ndipo tiyenda mumdima, tinama, ndipo siticita coonadi; koma ngati tiyenda m’kuunika, monga Iye ali m’kuunika, tiyanjana wina ndi mnzace, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wace utisambitsa kuticotsera ucimo onse. Tikati kuti tiribe ucimo, tidzinyenga tokha, ndipo mwa ife mulibe coonadi. Ngati tibvomereza macimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire macimo athu, ndi kutisambitsa kuticotsera cosalungama ciri conse. Tikanena kuti sitidacimwa, timuyesa Iye wonama, ndipo mau ace sakhala mwa ife.”
Kodi chinthu chofunikira ndi chotani kuti tikhale ndi nzeru yoyanjana ndi Mzimu Woyera?
Poyamba tiyenera kudziwa ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndi kuziyeretsa tokha kumachimo athu onse kudzera m’chikhulupiliro.
Ngati mukufuna kukhala mu chiyanjano ndi Mzimu Woyera, choyamba, muyenera kudziwa kuti ngakhale tchimo laling’ono pamaso pa Ambuye limapangitsa kuti chiyanjano chilephereke. Mungaganize kuti, ‘zingatheke bwanji kuti munthu akhale alibe tchimo ngakhale laling’ono pamaso pa Ambuye?’ Koma ngati mukufunadi kuyanjana ndi Ambuye ndiyeno muyenera kukhala mulibe mdima mu mtima mwanu. Chotero, kuti mukhale mu chiyanjano ndi Ambuye, muyenera kudziwa kuti muyenera kukhulupilira mu uthenga wabwino wa chiombolo ndi kuziyeretsa nokha kumachimo onse.
Ngati mukufunadi kuyanjana ndi Mzimu Woyera, ndiyeno muyenera kudziwa ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndi kuyeretsa machimo anu kudzera mu chikhulupiliro. Ngati simukudziwa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndipo simumautenge mu mtima wanu, ndiyeno simuyenera kuganizira za kukhala mu chiyanjano ndi Ambuye. Kukhala mu chiyanjano ndi Mzimu Woyera kumatheka pokhapo ngati machimo anu onse achoka mu mtima wanu kudzera mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Machimo onse angachoke mu maganizo mwa aliyense ndi choonadi Chake cha madzi ndi Mzimu. Ambuye amakudalitsani ndi Mzimu Woyera pamene mwakhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. Kodi mukufunadi kukhala mu chiyanjano ndi Ambuye ndi Mzimu Woyera? Ndiyeno zindikirani machimo anu ndipo khulupilirani mu uthenga wabwino okoma kuti muziyeretse nokha ku uchimo. Mukatero mungakhaledi mu chiyanjano ndi Ambuye.
Ngati mukufuna kukhala mu chiyanjano ndi Ambuye, muyenera kukhulupilira mu ubatizo umene Yesu analandira kwa Yohane mu Mtsinje wa Yordano ndiponso mukhulupilire mu mwazi Wake wa pa Mtanda. Ngati anthu akufunadi kukhala mu chiyanjano ndi Mzimu Woyera, ayenera kudziwa kuti Mzimu Woyera ndi chiyani. Mzimu Woyera ndi Woyera M’modzi. Ndipo motero ungakhale mwa onse amene akhulupilira mu uthenga wabwino okoma.
Tiyeni tione kuvomereza kwa munthu amene machimo ake anayeretsedwa pokhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi Yohane ndiponso mu mwazi Wake, ndipo amene tsopano ali mu chiyanjano ndi Mzimu Woyera.
“Kuli anthu ambiri osiyana mdzikoli ndipo aliyense amakhala ndi maganizo ake ndi njira yakenso. Ndinali m’modzi monga iwo. Ndinali ndi moyo wachikhalire ndiponso kuchokera pa uwana wanga, ndinkatsatira amai anga ku mpingo ndipo ndinayamba kukhulupilira mwa Mulungu. Atate anga anali osakhulupilira Chauta ndipo nthawi zambiri anali kundineneza chifukwa cha zikhulupiliro zanga, koma banja langa lonse linali kupita ku mpingo. Kupita kumpingo inali mbali yanga yaikulu mu moyo wanga.
Komabe, munthawi ya unyamata wanga, kuona atate anga ali chigonere, maganizo ambiri okhudza umoyo ndi imfa, Kumwamba ndi Gahena anabwera pa ine. Anthu ambiri ankanena kuti ngati ndinakhulupilira mwa Mulungu, ndikanatha kulowa Kumwamba ndi kukhala mwana Wake, koma sindinali otsimikiza za chimenecho. Sindinali otsimikiza kuti ndidzakhala mwana Wake. Ndinaphunzira kuti ngati ndingachite zabwino padziko lapansi ndiye kuti ndingalowe Kumwamba ndipo ndinayesa kuchita zabwino kwa osowa.
Koma kumbali imodzi ya mtima wanga, ndinali kudziwa kuti ndinali ochimwa. Ndinali kuoneka ngati munthu wabwino kwa ena koma sindinathe kusiya kudankhawa chifukwa cha machimo anga. Panthawiyo, ndinachipanga kukhala chizolowezi kupita kumpingo ndi kukapemphera, ‘Chonde ndiloleni ndikhaledi mwana Wanu, Chonde ndiloleni ndidziwe choonadi.’ Pamene ndinali kupemphera ndinayamba kukhala ndi chilimbikitso chatsopano mu m’mtima mwanga. Paliponse pamene ndamvetsera ku ziphunzitso za mawu Ake, sindinathe kumvetsetsa ngakhale kuona mawu. Ndinali otopa ndi kupanda kanthu kwa moyo wanga, uchimo wanga, imfa ndi zina zotere.
Ndinali ndi maganizo monga, ‘Ndifuna kubadwa mwatsopano. Ngati ndingabadwe mwatsopano, Sindidzakhala motere.’ Koma kupatula maganizo amenewa ndinali kupita kumpingo nthawi zonse ndipo zaka zanga zaunyamata zinapita. Tsopano ndinkafunika kupeza ntchito, koma zinali zovuta kuposa ndi m’mene ndikaganizira. Ndinali osakondwa ndipo ngakhale ndinayesera motani, sindinali kukhala wachimwemwe. Ndikaziyang’ana ndekha ndi mtima opanda kanthu, Ndinakhala mu mkhalidwe wachisoni. Pa nthawi imeneyo, Ndinamva uthenga wabwino kuchokera kwa mbale wanga wamkuru.
“Cifukwa cace lapani, bwererani kuti afafanizidwe macimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zocokera ku nkhope ya Ambuye” (Macitidwe a Atumwi 3:19). Uwu unali uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Zonse zimene Ndinkaphunzira ku mpingo wanga wakale zinali zakuti Yesu anafa pa Mtanda chifukwa cha machimo athu. Koma uthenga wabwino uwu unandiuza kuti Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi kuti achotse machimo athu ndipo anaweruzidwa pa Mtanda chifukwa cha machimo athu.
Ndinali kupita kumpingo moyo wanga onse ndipo ndinali kuonetsa ngati kuti ndine mwana wa Mulungu, koma ndinalephera. Ndinayesa kumvetsetsa tanthauzo la mawu Ake, koma ndinalephera. Komabe, pamene ndinamva uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu ndi kukhulupilira mwa uwo, uchimo mwa ine ndi zinthu zonse zimene zinkasautsa ine zinasowa ndipo mtima wanga unakhala pamtendere.
Ndinaganiza kuti ngati ndingakhulupilire mwa Mulungu yekha mwa chidwi ndi kupita kumpingo mokhulupirika, ndiye kuti ndizapita Kumwamba. Koma Mulungu ananditumizira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndipo machimo anga anakhululukidwa. Iye anandipatsa mphatso ya Mzimu Woyera. Ndisanalandire chiombolo Chake, sindinkadziwa za Mzimu Woyera kapena ganizo la kulankhula m’malilime. Ndinkangopita kumpingo ndi kukhulupilira kuti ngati ndingakhale molimbika ndi kutumikira mpingo wanga, ndiye kuti Mulungu adzandidalitsa. Koma Ndinazindikira kuti ndingalandire Mzimu Woyera pokhapo ngati machimo anga akhululukidwa kudzera mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu.
Mu moyo wanga wakale, ndinali mu uchimobe ngakhale kuti ndinali kukhulupilira mwa Mulungu. Ndipo ndinali kukhala ndi moyo monga wozizira kapena wotentha , osadziwa kufunika kwa kulandira Mzimu Woyera. Koma kudzera mwa kapolo Wake, amene analalikira uthenga wabwino okoma mogwirizana ndi Baibulo, ndinakhulupilira ndi kudziwa kuti Mzimu Woyera umakhalanso mwa ine.
Nditalandira chiombolo, poyamba ndinalibe chitsimikizo kuti kaya Mzimu Woyera unali mwa ine kapena ai. Koma Ndinapitiriza kuwerenga mawu Ake ndipo ndinazindikira kuti mu mtima wanga chikhulupiliro chatsopano chinali kukula ndiponso kuti ndinalandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Tsopano ndi zoona, ndipo ndikumva ndiri ndi chitsimikizo kuti Mzimu Woyera umakhala mwa ine! Pamene anandikhululukira machimo anga ndinadziwa kuti okhawo amene ali omasuka ku uchimo angakhaledi ana a Mulungu ndi kulandira Mzimu Woyera.
Ndinadziwanso kuti kuyesayetsa kwanga kuti ndioneke wangwiro m’maso Mwake kapena kukhala mwangwiro sikunandilole kuti ndilandire Mzimu Woyera. Mulungu amabwera ku iwo amene akudziwa kuti ndi ochimwa ndipo sakudziwa chochita pa zimenezo. Iye amakumana ndi iwo amene amamufunafuna mwa chidwi ndi kufuna Iye.
Iye anapanga ine kuona kuti kuchita zabwino ndi kukhulupilira mwa Mulungu mozitailira sikungandipereke Kumwamba ndiponso kuti Yesu Kristu anabwera padzikoli kudzandipulumutsa kumachimo anga kudzera mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. Iye anandipatsa Mzimu Woyera kuti ukhale mkati mwa ine kwamuyaya.
Ndikuyamika Ambuye pakundipanga kukhala mwana Wake ndi kundidalitsa ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Kuti sikunali kwa Ambuye, ndikanakhalabe ndi uchimo mu mtima mwanga ndipo ndikanaweruzidwira ku moyo wa mu ndende osatha mu Gahena.”
Chimodzimodzi, nthawi ina ndinakhulupilirapo mu mwazi okha wa pa Mtanda ndipo sindinalandire Mzimu Woyera ngakhale kuti ndinali kufuna. Pa nthawi imeneyo, Ndinkakhulupilira mwa Yesu, koma ndinali ndi uchimo mu mtima mwanga umene unali kundiletsa ine kuti ndilandire Mzimu Woyera. Ochimwa sangalandire Mzimu Woyera mu mtima wake. Komabe, ochimwa ambiri amayesa kulandira Mzimu Woyera ngakhale pamene mitima yawo ndi yodzala ndi uchimo.
Ngati mukufunadi kulandira Mzimu Woyera ndi kukhala mu chiyanjano ndi Iye, muyenera kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu ndi kupeza chiombolo. Kodi mudakali ochimwabe? Ndiyeno mungamvere uthenga wabwino oona kwa iwo amene analandira kale Mzimu Woyera. Iwo amene akufuna kuyanjana ndi Mzimu Woyera ayenera kukhala ndi mtima wa ludzu ndi kudalira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu.
Olungama okha ndi amene angamve mawu a Mzimu Woyera kudzera mu mpingo. Iwo angakhale ndi miyoyo yawo yachikhulupiliro mwa kumvera ku uthenga wabwino okoma, koma ochimwa amakhala miyoyo yawo yotembeleredwa yoyenera ku Gehena kopanda kumverapo uthenga wabwino.
Choncho, muyenera kuphunzira za uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Kodi chifukwa n’chiyani mukufunika kukhulupilira mu uthenga wabwino umenewu? Ndi kofunikira kwa inu kuti muthawe ku chipembezo cha lamulo ndi kumanga chikhulupiliro chanu mu uthenga wabwino okoma ochokera mu mawu a Mulungu. Ophunzira a Yesu anatsatira uthenga wabwinowu ndipo tsopano uli wa iwo amene alandira Mzimu Woyera. Uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu ndi ofanana kwambiri ndi uja umene anautsatira atumwi pachiyambi cha mpingo oyambirira. Akristu onse ayenera kulandira Mzimu Woyera. Pokhapo ndi pamene angakhale ana a Mulungu.
Onse amene asanakhulupilire mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu ayenera kukhala ndi uchimo mu mitima yawo. Iwo sangakhale mu chiyanjano ndi Mzimu Woyera. Kuti akhale mu chiyanjano ndi Iye, ayenera poyamba kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu umene Mulungu anapereka kwa iwo ndi kulandira Mzimu Woyera.
Baibulo mobwerezabwereza limatchula za Mzimu Woyera
Kukhazikika kwa Mzimu Woyera kunayamba Yesu ataukitsidwa. Tsopano ndi tsiku la chipulumutso ndipo tsopano ndi nthawi ya chisomo Chake chopanda malire. Koma ndi tsoka loona ngati sitilandira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndiponso ngati tikhala osayanjana ndi Mzimu Woyera.
Kodi muli mu chiyanjano ndi Mzimu Woyera? Kodi mukuletsedwa kukhala ogwirizana ndi Mzimu Woyera chifukwa cha machimo anu? Ndiyeno phunzirani za uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu umene Mulungu anapereka kwa inu ndipo ukhulupilireni. Ngati mukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, Mzimu Woyera udzakhala mu mtima mwanu ndipo udzakhala okuthangatani. Mzimu Woyera umakhala mwa okhawo amene akhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Mzimu Woyera kawiri kawiri umavumbulutsa chifuniro Chake mu mitima mwa olungama. Utumiki wa Paulo ndi Mzimu Woyera unali wa kufalitsa uthenga wabwino okoma.
Kodi mungamudziwe bwanji munthu amene analandira Mzimu Woyera? Kodi muyeso wake ndi chiyani? Muyeso wake ndi wakuti kaya amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu kapena ai. Ngati munthu akudziwa ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu, ndiye kuti ndi munthu amene ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera.
Mzimu Woyera sumakhala mwa iwo amene sakhulupilira mu uthenga wabwino okoma. Mzimu Woyera umakhala mwa okhawo amene akhulupilira mu chikhululukiro cha uchimo chimene chimachokera mu ubatizo wa Yesu umene analandira kwa Yohane ndiponso mu mwazi Wake wa pa Mtanda. Kodi mukufuna kuyanjana ndi Mzimu Woyera?
Kodi mukudziwa mtundu wa uthenga wabwino umene mufunika kumvetsetsa kuti mulandire Mzimu Woyera ndi kuyanjana ndi Iye? Uthenga wabwino okoma ukupezeka mkati mwa chikhulupiliro cha ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda. Ngati simukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, machimo anu sangakhululukidwe ndipo motero Mzimu Woyera sungakhale mwa inu. Mzimu Woyera ukufuna kuti anthu ayenera kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu kuti amlandire Iye.
Mzimu Woyera sungakhale mkati mwa mitima ya ochimwa. Ngati mukufuna kulandira Mzimu Woyera, muyenera poyamba kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma kuti mudziyeretse nokha ku machimo anu onse. Ndiponso, ngati mukufuna kukhala mu chiyanjano ndi Mzimu Woyera, muyenera kukhala okhulupirika mu kulalikira uthenga wabwino okoma. Ngati mukufuna kutsogoleredwa ndi Mzimu Woyera, muyenera nthawi zonse kukonda uthenga wabwino okoma ndi kufuna kuufalitsa kulikonse kumene mungapite. Mzimu Woyera uli ndi iwo amene amalalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Kukhazikika kwa Mzimu Oyera kumaperekedwa kwa okhawo amene akhulupilira mu uthenga wabwino okoma. Olungama okha, onse a iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma okha, ndi amene angakhale mu chiyanjano ndi Mzimu Woyera. Uthenga wabwino okoma umene Mzimu Woyera umatsimikiza ndi uthenga wabwino umene unakwaniritsidwa mwa ubatizo wa Yesu ndi Yohane ndi mwazi Wake (1 Yohane 5:3-7).
Petro nayenso anakhulupilira mu uthenga wabwino okoma ndipo anati, “Cimenenso cifaniziro cace cikupulumutsani tsopano, ndico ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lace la thupi, komatu funso lace la cikumbu mtima cokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Kristu” (1 Petro 3:21). Mu Baibulo, “madzi” mobwerezabwereza amaimira ubatizo umene Yesu analandira kwa Yohane Mbatizi.
Onse a iwo amene angathe kulandira Mzimu Woyera analandira chiombolo kudzera mu uthenga wabwino okoma ndipo ndi omasuka ku uchimo onse. Onse amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma angalambire Atate mu mzimu ndi m’choonadi motsogoleredwa ndi Mzimu (Yohane 4:23). Mzimu Woyera umathandiza olungama kukhala ndi umoyo wawo odzala ndi Mzimu Woyera. Onse a iwo amene ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera angakhale kwamuyaya akutamanda Ambuye. Mzimu Woyera umanena kuti ndife ana a Mulungu. Tingakhale kwamuyaya mkati mwa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndiponso mkati mwa Mzimu Woyera.
Mzimu Woyera Sumakhala mu chiyanjano ndi iwo amene akuzinyenga iwo okha
Mzimu Woyera umauza ochimwa mu 1 Yohane 1:8, “Tikati kuti tiribe ucimo, tidzinyenga tokha ndipo mwa ife mulibe coonadi .” Mzimu Woyera sungakhale mwa iwo amene amazinyenga okha. Mzimu Woyera umachenjeza ochimwa, kunena kuti, “Kodi chifukwa chiani simunakhulupilire mu uthenga wabwino okoma unamalizidwa ndi ubatizo wa Yesu komanso mwazi Wake?”
Tizaona pa kuvomereza kwa mKristu obadwa mwatsopano amene anakhulupilira poyamba kuti analandira ndi Mzimu Woyera alibe umboni wa ubatizo wa Yesu komanso mwazi Wake. Munthu ameneyu tsopano amakhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi mwazi ndipo walandira Mzimu Woyera. Apa, tiyenera kuloza ndendende kuti Mzimu Woyera umakhala mwa ndani.
“Mulungu anayamba kukhala mu mtima mwanga pamene ndinazindikira chifukwa chimene ine ndinapezekera m’dziko lino. Ndikaziona ndekha, ndikuganizira ndekha kufoka kwanga kokhala m’dziko lankhanzali kunachoka monga chilakolako kwa Mulungu. Sindinafunefune Mulungu koma mwachibadwidwe ndinalola kupezeka kwake pakuti Iye ndiosaoneka, koma Iye aliko. Indedi, ndimazifunsa ndekha, ‘Kodi zoona aliko?’ koma ngakhale ganizo la ilo limandiopseza popeza ndinakhulupilira zolimba kuti Iye ndi Mlengi wa onse.
Iwo amene anakana Mulungu anaoneka opusa, koma m’njira zina ndi amphamvu kuposa ine. Anaoneka ngati angakwanitse pachilichonse pa iwo okha ndipo kumbali ina ndinkaoneka ngati ofoka opusa. Koma chifukwa ndinali ndi ziyembekezo zakuti kuli moyo pambuyo pa imfa, ndinayang’ana kwa Mulungu ngakhale ndi ulemu waukulu. Ndinadzizwa kuti mwina Kumwamba anali malo a anthu monga ine amene ndikuzimva kuti nthawi zonse amakhala osoweka. Ndipo funso limenelo linapangitsa ine kufuna motsimikizira paradaiso wa Kumwamba.
Makolo anga ankanyoza anthu ali a chipembezo ndipo alongo anga anali kupita ku mpingo mosalimbikira. Anali kuganiza kuti kulimbikira kwanga kumpingo kuzafa mwamsanga ndipo sanafune kundiletsa kupita kumpingo kufikira Nditafika sukulu lapakati. Choncho Ndinkapita ku mpingo uwu ndi uwo ndipo pomaliza ndinayamba kumapita kumpingo waung’ono pafupi ndi nyumba yanga kufikira nditafika ku sukulu yapamwamba.
Chifukwa chimene ndinasankhira kupezeka pampingo umenewu chinali chakuti unaika chisindikizo mu uthenga wabwino. Mbusa wa mpingowo anali mlaliki wa chitsitsimutso amene sankachita chilichonse koma kuononga mawu a m’Baibulo. Ndinali ndi chifukwa chokhalila moyo wa chipembezo mofunitsitsa, ngakhale pamene ndinali ndi nkhawa komanso ofoka ndi maphunziro anga.
Chifukwa chinali chakuti pamene anthu anali kuitana mamembala anzanga kuti akunja, ndinali kukhulupilira kuti mpingo wanga unali bwino ndipo ndinali ndichiyembekezo kuti ndizapita Kumwamba. Chiyembekezocho chinaimilira pa uthenga wabwino. Iwo anali kunena kuti ochimwa sangalowe pa zipata za Kumwamba, koma anthu a mipingo ina naonso anali kunena kuti mitima yawo inali yodzala ndi uchimo. Inenso ndinakhulupilira kuti anthu a mpingo wanga anali ochimwa ndisanapezeke ku mpingo, choncho sindinaganizire kwambiri za kutsutsa kumeneko.
Koma iwo amene ankazitcha kuti alaliki a chitsitsimutso anali osiyana ndi zimene ndinaona kale. Iwo anali kunena kuti ngati tingakhulupilire mwa Yesu mukhalidwe labwino, tinali opanda tchimo. Ndipo okhawo amene ali opanda tchimo ndi amene angapite Kumwamba. Iwo ananenanso kuti Yesu anatipatsa chilungamo pa Mtanda ndipo motero sitinali ochimwa koma anthu olungama. Poyamba sindinakhulupilire zimenezi, koma pamene ndinaganizirapo, zinapanga nzeru. Ndinali wamng’ono, ndipo ndinaganiza kuti ngati ndikufuna kupita Kumwamba, Mulungu adzandilola kulowa pokhapo ngati ndinali osachimwa, popeza Mulungu amadana ndi uchimo.
Mpingo umenewu uli ndi zikhulupiliro zosiyana ndi zimene ndinali nazo, ndipo mwambo wakupembeza unali osiyananso pang’ono. Koma chifukwa Kumwamba ndi malo kumene okhawo osankhidwa ochepa angalowe, zinaoneka ngati anthu a mu mpingowu anali atapeza zikhulupiliro zabwino. Chifukwa mpingo umadera nkhawa thupi la Yesu ndi mwazi, Sabata lililonse timaluma mkate ndi kumwa vinyo. Chifukwa chikondwerero chimenechi chinali kuchokera m’mawu a Baibulo, ndinachivomereza. Koma pamapeto pake ndinapeza kuti anthu anali kutengako mbali mu mwambo okha kopanda kumvetsetsa tanthauzo lake lenileni.
Ndinakhulupilira kuti Mzimu Woyera umakhala mu mitima ya okhulupirika ndi mu mitima ya olungama ndipo kuti amamvera mapemphero awo. Choncho Ndinakhulupilira kuti Mzimu Woyera unakhalanso mwa ine. Ndinali otsimikizira kuti Mulungu anali bwenzi langa ndipo sindinakaikirepo uthenga wabwino umene ndinali kukhulupilira. Pamene Ndinali kupita mu nthawi zovuta, ndinkalankhula ndi Mulungu ngati kuti anali pafupi ndi ine. Ndinakhulupilira kuti anali kumvera kwa ine pamene ndinali kumuuza zinthu zimene sindinali kuuza wina aliyense. Choncho ndinakhulupilira Iye ndiponso ndinadalira mwa Iye.
Sindinkawamvetsetsa iwo amene anali kupita kumisonkhano yachitsitsimutso kukalankhula m’malilime ndipo ndinali kuseka iwo amene anali kupezeka pa mapemphero a kusala kudya. Kuyang’ana pa mphamvu zotere ndinaganiza, “Kodi chifukwa n’chiyani amapita ku mphamvu zopanda tanthauzo kukalandira Mzimu Woyera? Mzimu Woyera umabwere kwa iwo pokhapo ngati ndi osachimwa ndi kukhala nawo nthawi zonse. Ayenera kukhala ochimwa. Sadzabwera kwa iwo angakhale mwa mphamvu zawo zonse.’ Ndinawamvera chisoni iwo. Ndinaganiza kuti anali opusa kwambiri. Ndi maganizo anga motero, Ndinaganiza kuti chikhulupiliro changa mu uthenga wabwino chinali chabwino koposa ndipo zikhulupiliro zina zonse zinali zabodza.
Mtima wanga waumbuli unapyola muyeso. Kwa zaka 10 Ndinakhala moyo wachipembezo pa ine ndekha. Koma pamene nthawi inapita mafunso anayamba kubwera m’maganizo anga ndi mu mtima mwanga. Ndinaganiza kuti, ‘Ndine osachimwa chifukwa cha uthenga wabwino wa mwazi wa pa Mtanda, koma kodi okhulupilira ena naonso ndiwosachimwa? Kodi naonso amakhulupilira mu uthenga wabwino umenewunso?’ Sindinadziwe chifukwa ndinayamba kuzifunsa mafunso amenewa. Mafunso anangobwera m’maganizo anga ndipo sindinafunse aliyense. Ichi chinali chikhulupiliro cha munthu yekha ndipo sichinayenera kusokonezedwa. Ndipo likanakhala funso lachipongwe kufunsa wina aliyense.
Koma ndinayamba kuzifunsa mafunso amenewa ine ndekha. Pamene ndinali ku sukulu yapamwamba, ndinayamba kuchita zinthu zimene zinali zoletsedwa ndi malamulo a chipembezo ndipo mtima wanga unakhala wakuda kotero kuti zikhulupiliro zanga zinayamba kuchoka. Sindinalinso otsimikizira za zikhulupiliro zanga. ‘Kodi ndingaziitane ndekha kuti munthu olungama? Kodi Yesu anandiyeretsadi machimo anga onse?’ pakatikati ka msokonezo onsewu, ndinazikakamiza kuganizira za uthenga wabwino wa pa Mtanda ndipo ndinatsuka maganizo anga ndi umenewu. Koma pamene ndinkazikankha ndekha kwambiri, ndi pamene ndinkalepheranso kwambiri, ndipo sindinalinso kupezeka ku mpingo. Ndinali kugwiritsira ntchito zochitika za makalabu ngati chifukwa chake.
Chifukwa cha msokonezo onse ndi zovuta, pothera pake ndinapeza choonadi. Ndinamva za uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndipo unabwera kwa ine ngati mphenzi. Zotsatira zake zinali zazikulu kotero kuti ndinazimva ngati ndingalire. Koma kumvera ku uthenga wabwino, ndinayenera kuvomereza kuti zonse zimene ndinali kukhulupilira kufikira pamenepo zinali zabodza.
Sindinapereke machimo anga kwa Yesu. Ndinakhulupilira mosadziwa kuti anachotsa machimo anga ndipo kuti ndinali munthu osachimwa, koma umo sim’mene zinalili. Kodi chifukwa ndi chiyani Yesu anabwera padziko lapansi ndi kubatizidwa? Chifukwa anali kufuna kutionetsa kuti anali odala ngati mwana wa nkhosa. Kuonetsa kuti anabwera ngati munthu? Kapena kuzanenera za imfa Yake yosayembekezereka? Sindinalotepo kuti nzeru iliyonse yosadziwika ya ubatizo imene ndinali nayo inali yofunikira. Choonadi chinali chakuti Yesu anabatizidwa ndi Yohane, woimilira mtundu onse wa anthu, ndipo ndi ubatizo umenewo, machimo athu onse anaperekedwa kwa Iye.
‘Oho! Ndi chifukwa chake Yesu anakhala Mwana wa Nkhosa wa Mulungu amene ananyamula yekha machimo athu onse!’ Tsopano zilizonse zinapanga nzeru. ‘Yesu anaweruzidwa chifukwa cha machimo anga pa Mtanda. Ndi chifukwa chake ndiribe tchimo mu mtima mwanga.’ Pamene ndinadziwa za uthenga wabwino wa madzi (ubatizo wa Yesu), mwazi (Mtanda), ndi Mzimu Woyera (Yesu ndi Mulungu), machimo amene ndinali kumva mu mtima mwanga anachoka.
Tsopano ndinedi osachimwa ndiponso munthu olungama ndipo Mzimu Woyera potsiriza umakhala mu mtima wanga. Chikhulupiliro chomwe ndinali nacho mu Mtanda sichinali chokwanira kundiyeretsa kumachimo ndinali nawo mu mtima wanga. Ngati simukudziwa bwinobwino m’mene machimo anu anaperekedwera kwa Yesu, machimo anu sangakhululukidwe, ndipo Mzimu Woyera sungakhale mwa inu. Ndikuyamika Ambuye. Ndinatha kulandira Mzimu Woyera kudzera mu uthenga wabwino okoma.
Kopanda mphamvu yanga iliyonse, ndinakhululukidwa kudzera mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndipo Mzimu Woyera umakhala mwa ine tsopano ndiponso kosatha. Tsopano, ndingazitche mozikuza kuti munthu osachimwa ndipo ndingakhale onyadira kuti Ufumu wa Kumwamba ndi wanga. Ndikutenga mpata umenewu kuyamika Ambuye chifukwa cha kundipatsa madalitso amenewa kopanda malipiro. Aleluya!”
Iwo amene analandira Mzimu Woyera anganene kuti ndi osachimwa pamaso pa Mulungu. Ziribe kanthu kuti mwakhala okhulupirira mwa Yesu kwa nthawi yotani, ngati simunakhulupilire mu uthenga wabwino okoma umene Mulungu anatipatsa, mulidi ndi uchimo mu mtima wanu. Anthu otero akuzinyenga okha komanso Mulungu. Anthu amenewa sanakumanepo ndi Ambuye. Ngati ochimwa akufuna kukhala mu chiyanjano ndi Mzimu Woyera, ayenera poyamba kusiya kuzinyenga yekha ndi kuvomereza kuti anachimwa. Pokhapo kutero ndi pamene angayenere kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma umenewu ayenera kulandira Mzimu Woyera.
Kodi Mzimu Woyera umanena chiyani kwa ochimwa? Amawachenjeza kuti apeze chikhululukiro cha machimo awo mwa kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma umene unakwaniritsidwa ndi ubatizo wa Yesu ndiponso mwazi Wake. Ngati mukunena kuti sindinu ochimwa pamene munachimwa, ndiye kuti simuzalandira Mzimu Woyera. Iwo amene sakhulupilira mu uthenga wabwino okoma ndi kunena kuti sanachimwepo akuzinyenga okha komanso Mulungu. Ochimwa ayenera kudziwa za uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu ndi kulandira Mzimu Woyera. Pokhapo kutero ndi pamene angaomboledwe ku chiweruzo chowawa cha Mulungu.
Olungama angakhale mu chiyanjano ndi Mzimu Woyera mwa Kuvomereza machimo awo
Ndikunena kwa iwo amene amakhulupilira mu uthenga wa madzi ndi Mzimu ndipo motero, alandira Mzimu Woyera. Tiyeni tione pa zimene Mulungu anauza olungama. Mu 1 Yohane 1:9, akunena kuti, “Ngati tibvomereza macimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire macimo athu, ndi kutisambitsa kuticotsera cosalungama ciri conse.” Ndimeyi ikutanthauza kuti tingayeretse machimo athu enieni ku mitima yathu yodetsedwa mwa kuzikumbutsa tokha ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma umene ukunena kuti Yesu ananyamula machimo athu onse pamene Iye anabatizidwa ndipo anawatetezera iwo mwa kupachikidwa. Olungama ayenera kuvomereza machimo awo amasiku onse kwa Mulungu. Pokhapo ndi pamene angakhale mu chiyanjano ndi Mzimu Woyera. Olungama ayenera kuvomereza machimo awo amasiku onse ndi kupitiriza kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma.
Kalekale, uthenga wabwino okoma wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake unayeretsa machimo athu onse ndipo chotero, olungama ayenera kukhulupilira mu uthenga wabwino ndi kukhala omasuka ku machimo awo onse. Ambuye anakhululukira kale machimo awo onse kudzera mu uthenga wa madzi ndi Mzimu. Olungama ayenera ukhulupilira mu uthenga wabwinowu okoma kuti amasuke ku machimo awo. Olungama angayeretse mitima yawo mwa kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu ngati adetsedwa ndi machimo awo amasiku onse.
Ambuye wathu anayeretsa kale machimo onse a olungamo kalekale mwa ubatizo Wake ndi mwazi Wake. Choncho, iwo amene amakhulupilira ndi omasukadi kumachimo awo onse. Komabe, olungama ayenera kuvomereza ndi kuvomera machimo awo pamaso pa Mulungu. Ndipo kenako olungama ayenera kubwerera kuchikhulupiliro cha mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, umene ndi uthenga wabwino okoma, pofuna kukhala omasuka kumachimo awo onse. Choncho, nthawi zonse angakhale moyo watsopano otsatira Mzimu Woyera. Iwo amene angathe kuyang’ana kwa Ambuye kopanda kudera nkhawa za kufoka kwawo angakhale mu chiyanjano choona ndi Mulungu tikuthokoza ku uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu.
Kodi tingapeze motani nzeru yoona ya chiyanjano ndi Mzimu Woyera?
Pali anthu ambiri amene amafuna kukhala mu chiyanjano ndi Mzimu Woyera. Koma sakudziwa m’mene angachitire kuti chifunirochi chikhale chotheka, ngakhale kuti amakhulupilira mwa Yesu. Anthu onse amalandira Mzimu Woyera mwa kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndi kuyamba kukhala mu chiyanjano ndi Mzimu Woyera kuyambira pa nthawi imeneyo.
Chimodzimodzi, njira yokhayo imene munthu olungama angakhalire mu chiyanjano ndi Mzimu Woyera ndi mwa kudziwa ndi kukhulupilira choonadi cha uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Chiyanjano pakati pa olungama ndi Mzimu Woyera sichingakwaniritsidwe popanda uthenga wabwino oona. Kodi nanga bwanji za chiyanjano ndi Mzimu Woyera? Kungatheke pokhapo mwa kukhulupilira mu choonadi cha uthenga wabwino okoma.
Mulungu amanena kuti munthu amachimwa moyo wake onse
Mu 1 Yohane 1:10, akuti, “Tikanena kuti sitidacimwa, timuyesa Iye wonama, ndipo mau ace sakhala mwa ife.” Sipakanakhala aliyense amene sankanachimwapo pamaso pa Mulungu. Ngakhale Baibulo limanena kuti, “Pakuti kulibe wolungama pansi pano amene acita zabwino osacimwa” (Mlaliki 7:20). Anthu onse amachimwa pamaso pa Mulungu. Ngati wina wake amanena kuti sanachimwepo, ndiye kuti ndi wabodza. Anthu amachimwa moyo wawo onse kufikira nthawi ya kufa kwawo ndipo ndi chifukwa chake Yesu anabatizidwa ndi Yohane kuti anyamule machimo awo onse. Kukanakhala kuti sitiachimwe, ndiye kuti sitikanafunika kukhulupilira mwa Mulungu ngati Mpulumutsi wathu.
Ambuye amanena kuti, “Mawu anga sali mwa inu” kwa iwo amene amaganiza monga ngati sanachimwepo. Ngati munthu alibe chikhulupiliro mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu, ndiye kuti ayenera chionongeko. Ngati munthu olungama kapena ochimwa akunena kuti sanachimwepo pamaso pa Mulungu, ndiye kuti sayenera kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma.
Ambuye anapatsa aliyense mphatso yabwino ya uthenga wabwino okoma. Tinavomereza machimo athu onse ndipo tinalapa pofuna kuti tilandire chikhululukiro cha machimo pamodzi ndi uthenga wabwino okoma. Tingabwerenso ku uthenga wabwino okoma umene Mulungu anaika pa ife ngati chikhululukiro cha machimo athu ndi kukhulupilira mwa iwo pofuna kuti tikhale mu chiyanjano ndi Mzimu Woyera. Nzeru yoona ya chiyanjano ndi Mzimu Woyera ili mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, ndipo ndi okhawo amene ali ndi uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndi amene angagwirizane ndi Mulungu.
Mtundu wa anthu unali kutali ndi Mulungu chifukwa cha machimo anatenga kwa Adamu ndi Hava. Koma tsopano ife, amene tinatenga mbewu ya uchimo, tingayang’ane patsogolo kuti tiyanjanenso ndi Mulungu. Kuti tichite choncho, tiyenera kubwerera ku chikhulupiliro cha uthenga wabwino wa Yesu Kristu wa madzi ndi Mzimu ndi kukhululukidwa machimo amene anatiika kutali ndi Mulungu.
Iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma adzapulumutsidwa ku machimo awo onse ndipo Mulungu adzawadzadza ndi Mzimu Woyera. Olungama angakhale mu chiyanjano ndi Mulungu, popeza analandira Mzimu Woyera. Choncho, iwo amene anadulidwa kwa Mulungu chifukwa cha machimo awo ayenera kubwerera ku uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu ndi kukhulupilira mwa uwo. Pokhapo pakutero ndi pamene angayambe kukhala mu chiyanjano choona ndi Iye.
Kukhazikika kwa Mzimu Woyera kumabwera limodzi ndi chikhulupiliro mu uthenga wabwino okoma. Tiyenera kudziwa kuti kukhazikika kwa Mzimu Woyera kumabwera kudzera mu kukhulupilira kokha mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma kumapanga njira yatsopano yopita kwa Mulungu. Ambuye anaphwanya khoma lapakati limene linali kutilekanitsa kwa Iye chifukwa cha tchimo lachibadwidwe ndi machimo amasiku onse, ndi kutilola kuti tikhale mu chiyanjano ndi Mulungu kudzera mu chikhulupiliro chathu mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu.
Tiyenera kukhazikitsanso chiyanjano ndi Mzimu Woyera. Chiyanjano choona ndi Mzimu Woyera chimakwaniritsidwa kudzera mu kumvetsetsa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu chifukwa cholemekeza chikhulupiliro. Chiyanjano ndi Mzimu Woyera chimachitika ngati tili ndi chikhulupiliro mu choona cha chikhululukiro cha machimo athu chochokera ku uthenga wabwino okoma. Iwo amene asanalandire chikhululukiro cha machimo awo sangakhale mu chiyanjano ndi Mzimu Woyera. M’mawu ena, palibe amene angakhale mu chiyanjano ndi Mzimu Woyera kopanda kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Ngati ndi kovuta kwa inu kuti mukhale mu chiyajano ndi Mzimu Woyera, ndiyeno muyenera poyamba kuvomera kuti simukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndi kuti machimo anu sanakhululukidwe. Kodi mukufuna kuyanjana ndi Mzimu Woyera? Ndiyeno khulupilirani mu uthenga wabwino umene unakwaniritsidwa kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Pokhapo mukatero ndi pamene mudzakhululukidwa machimo anu onse ndipo ngati mphatso mudzalandira Mzimu Woyera mu mtima mwanu. Uthenga wabwinowu okoma ungakupatsenidi chiyanjano ndi Mzimu.