(Mateyu 25:1-12)“Pomwepo Ufumu wa Kumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi, amene anatenga nyali zao, naturuka kukakomana ndi mkwati. Ndipo asanu a iwo anali opusa, ndi asanu anali ocenjera. Pakuti opusawo, m’mene anatenga nyali zao, sanadzitengerenso mafuta; koma anzeruwo anatenga mafuta m’nsupa zao, pamodzi ndi nyali zao. Ndipo pamene mkwati anacedwa, onsewo anaodzera, nagona tulo. Koma pakati pa usiku panali kupfuula, Onani, mkwati! Turukani kukakomana naye. Pomwepo anauka anamwali onse amenewo, nakonza nyali zao. Ndipo opusa anati kwa ocenjera, tipatseniko ena a mafuta anu; cifukwa nyali zathu ziri kuzima. Koma ocenjera anayankha nati, Kapena sangakwanire ife ndi inu; koma makamaka mukani kwa oguritsa malonda mukadzigulire inu nokha. Ndipo pamene iwo analikumuka kukagula, mkwati anafika; ndipo okonzekawo analowa naye pamodzi muukwati; ndipo anatseka pa khomo. Koma pambuyo pace anadzanso anamwali enawo, nati, Mbuye, Mbuye, mutitsegulire ife. Koma iye anayankha nati, Indetu ndinena kwa inu, sindikudziwani.”
Kodi ndidani amene amaimiliridwa ndi anamwali amene ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera?
Kodi Mzimu Woyera umabwera kwa ndani?
Uwo umabwera kwa iwo amene akhululukidwa ku machimo awo pokhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake.
Mundime ili pamwambapa, muli anamwali asanu ochenjera ndi asanu opusa. Opusa asanu aja akupempha asanu ochenjera kuti awagawileko mafuta awo. Koma ochenjera anauza opusa aja nati, “Kapena sangakwanire ife ndi inu; koma makamaka mukani kwa oguritsa malonda mukadzigulire inu nokha.” Choncho, pamene opusa aja anapita kukagula mafuta, anamwali ochenjera asanu aja amene anali nawo mafuta a nyale zawo analowa m’nyumba imene munali phwando laukwati. Nanga kodi tingakonze motani mafuta a Ambuye? Chinthu chokhacho chimene tifunika ndi kumudikira Iye ndi chikhululukiro cha machimo m’mitima yathu.
Titha kupeza mitundu iwiri ya chikhulupiliro pakati pa anthu. Chimodzi ndi chikhulupiliro chili mu uthenga wabwino wa chikhululukiro cha machimo. Ichi chimatsogolera ku kulandira Mzimu Woyera. Chinacho ndi kungokhala wokhulupirika kwa zikhulupiliro za chipembezo za yekha-–osasamala kuti kaya Ambuye akhululuka machimo ake kapena ai.
Kwa iwo amene ali okhulupirika ku zokhulupilira zawo, uthenga wabwino wokoma umakhalabe wolemetsa. Monga anamwali opusa amene anapita kukagula mafuta pamene mkwati anali kubwera, iwo amene amachoka m’nyumba imodzi yopembezeramo kupita kwina ndi chiyembekezero cholandira Mzimu Woyera sakunamiza wina koma iwo wokha. Anthu otere ndi mbuli mu chilungamo chakuti iwo ayenera kukhala ndi chikhulupiliro mu uthenga wabwino okoma m`mitima yawo Tsiku la Chiweruzo lisanafike. Iwo amafuna kulandira Mzimu Woyera pakukondweretsa Mulungu ndi kudzipereka kwao. Tizayang’ana pa zakuvomereza kwa dikoni wina wothandizira amene anachita molimbika kuti alandire Mzimu Woyera. Kuvomereza uku kuzakhala ndi phindu kwa inu.
Ndinachita chilichonse kuti ndilandire Mzimu Woyera. Ndinaganiza kuti ngati ndazipereka kuchikhulupiliro changa mwachidwi, ndingalandire Mzimu Woyera ndipo choncho ndinali kuchoka m’nyumba ina ya mapemphero kupitanso kwina. Anthu a imodzi mwa manyumba ya mapemphero anali kusewera malimba amagetsi ndi ng’oma ngati mbali ya msonkhanowo. Abusa amene ankatsogolera msonkhano anaitana iwo amene ankafuna kulandira Mzimu Woyera m’modzi m’modzi ndipo pamene analikumenya mbama pamphumi pa munthuyo, anayamba kulankhula m’malilime. Anathamanga mozungulira ndi chikunza mau ndi kufuula “Landira moto, moto, moto” ndipo anaika manja ake pa mitu ya anthu, kupangitsa ena kukhunyuka ndi kukomoka. Ndinali ndi zikaiko pa zoti mchitidwe uwu unali pakulandira Mzimu Woyera koma ndinali nditazolowera kale kumisonkhano imeneyi. Kupatula zonsezi, sindinakwanitse kulandira Mzimu Woyera.
Pambuyo pokumana ndi izo, ndinapita kumapiri ndi kuyesa kulila ndi kupemphera usiku onse kwinaku nditagwira ku mtengo wa mkunguza. Ndipo ndinayesa kupemphereranso mu mphanga koma icho nachonso sichinagwire ntchito. Pambuyo pa izi, ndinayesa kupemphera usiku wonse kwa masiku 40 koma sindinakwanitse kulandira Mzimu Woyera. Kenako tsiku lina ndinaitanidwa ku msonkhano wina pa za Mzimu Woyera. Msokhano unali kukhalako kamodzi mu sabata, ndipo unkakhala kwa masabata asanu ndi awiri.
Msonkhano unali pa za chikondi cha Mulungu, Mtanda, kuuka kwa Yesu, kuika kwa manja, chipatso cha Mzimu, ndi kukula muuzimu. Pa nthawiyo pamene ndondomeko ya msonkhano inafika kumapeto, mlaliki mu msonkha uja anaika manja ake pamutu panga ndi kupempherera Mzimu Woyera, ndipo ndinachita zimene anandiuza. Ndinadekha ndi kuimika manja anga m’mwamba ndi kufuula mokweza kuti “la-la-la-la” mobwereza bwereza. Mwadzidzidzi, pamene ndinali kufuula “la-la-la-la” ndinayamba kulankhula momveka bwino mchilankhulo china. Anthu ambiri anandiyamikira pakulandira Mzimu Woyera. Koma pamene ndinali ndekha kunyumba, ndinali ndi mantha. Choncho, ndinayamba kugwira ntchito ngati wothandizira wa msonkhano. ndinaganiza kuthandizira pa ntchito zambiri motero ndinayenda yenda m’dziko kuti ndipereke ntchito zanga. ndipo ndinaika manja anga pa odwara ena, matenda awo anali kuoneka monga achila, ngakhale kuti anali kubwereranso pambuyo pake. Ndipo kenako ndinali ndi masomphenya m’maso mwanga ndipo ndinapeza kuti ndinali kunenera. Modabwitsa, uneneri wanga mthawi zonse unali kukhala oona. Kuchokera pa nthawi iyo, ndinkaitanidwa ku malo osiyana siyana ndi kusamalidwa ngati wotchuka. Koma ndinali ndi mantha ndithu. Kenako tsiku lina, ndinamva mau akuti, “Usamazungulira kuchoka malo amodzi kupita kwina motere, m’malo mwake pita ukathandize banja lako kuti lilandire chipulumutso.” Komabe, sindinkadziwa kuti chipulumutso ndi chiani. Ndinali kudziwa chabe zimene ena anandiuza - kuti ngati sindingagwiritse ntchito mphatsoyi ya Mzimu Woyera, Iye azandilanda. Ku mbali ina, ndinali kuopa kugwiritsa ntchito maluso anga komabe sindinasiye kuchita choncho.
Tsiku lina, ndinamvera kuti sing’anga wina wamkazi anali kufuna kukhuluplira mwa Yesu ndipo paicho ndinamyendera ndi anzanga. Sitinamudziwitse poyamba kuti tidzakhala mlendo wake. Koma sing’anga wamkazi uja anali kutidikira kale pabwalo pa chipata chake ndipo anati, “Ndinalikudziwa kuti mudzabwera. Kenako mwadzidzidzi anayamba kutiwaza madzi ndi kunena kuti, “Palibe kusiyana ndi zamatsenga za Kummawa ndi zamatsenga za Kummadzulo!” Iye anaticha ife asing’anga a Yesu,” anatiloza ndi kulankhula kuti, “Munthu uyu ndiwoopsa, koma osati uyo.” Zimene sing’anga wamkazi analankhula zinadza ngati nkhonya kumutu. Ndinayamba kuganiza kuti zonse zimene ndakhala ndikuchita sizinali zosiyana ndi zimene sing’anga amachita. Zonse zimene ndinachita panalibe chomwe chinandibweretsera Mzimu Woyera chifukwa ndinali ndi uchimobe mu mtima mwanga.”
Kuchokera mwa kuvomereza uku, taphunzira kuti kulandira Mzimu Woyera ndikopyora maluso athu. Chifukwa chikhulupiliro chotere sichichokera pa uthenga wabwino wa Mulungu, iwo amene amakhala moyo wachipembezo cha mtundu uwu alibe mafuta mnyale zawo.
Nyale mu Baibulo imatanthauza mpingo ndipo mafuta amatanthauza Mzimu Woyera. Baibulo limanena kuti iwo amene amapita kukachisi, kaya ndi mpingo wa Mulungu kapena ai, popanda kulandira Mzimu Woyera ndi opusa.
Opusa ndi otengeka kutenthetsa zikondi zawo zachipemebezo ndi kufunitsitsa kwao tsiku ndi tsiku. Kulankhula mosiyana, opusa akutenthetsa zomvera zawo pamodzi ndi kufunitsitsa kwao kwakhungu kwa Mulungu. Kukanakhala kuti tinalankhula kuti zomvera zathu zinali 20cm ndipo zimatengera tsiku limodzi kuti titenthepo 1cm, ndiye kuti zinakatenga masiku 20 okha kuti titenthe zomvera zathu zonse mumoto. Zomvera zawo kumbuyo kwa chikhulupiliro chawo zimakhala ndi mphamvu zatsopano kudzera m’mapephero a m’mawa, mapemphero ausiku wonse, mapemphero osala kudya ndi misonkhano ya chitsitsimutso, koma zomvera zawo zimatentha moyo wao wonse. Iwo anazolowera ku m’chitidwe umenewu osatha otenthetsa zomvera zawo zokha.
Zomvera zawo zimatenthedwa mdzina la Yesu. Iwo amapita kukachisi ndi kutenthetsa zomvera zawo koma mitima yawo idakali yosokonezekabe ndipo imafunana chinthu china. Chifukwa cha izi ndi chakuti chikhulupiliro chawo chimachokera ku zokumana nazo zakuthupi; motere, amafunika kawirikawiri kulimbikitsanso zimene akumva ndi cholinga choti lawi lisafe. Komabe, sangalandire Mzimu Woyera ndi chikhulupiliro chotere. Kutenthetsa zomvera zawo sikungawatengere kukulandira Mzimu Woyera.
Tonsefe tiyenera kukonza chikhulupilira choyenera kuti tilandire Mzimu Woyera mwathunthu pamaso pa Mulungu. Kenako ndi pokhapo pamene tidzayenera kulandira Mzimu Woyera. Kodi timapeza motani chikhulupiliro chomwe chimatipanga oyenera kulandira Mzimu Woyera? Choonadi chili mu uthenga wabwino okoma umene unakwaniritsidwa mwa ubatizo Yesu mu Mtsinje wa Yordano ndi kukhetsa kwa mwazi Wake pa Mtanda.
Mulungu amatitchula kuti, “Mbeu za yakucita zoipa” (Yesaya 1:4). Tifunika kubvomereza ichi kwa ife tokha. Anthu pachiyambi amabadwa ndi mitundu 12 ya machimo (Marko 7:21-23). Anthu saleka kuchimwa kuchokera pa tsiku limene anabadwa mpaka pa tsiku lakufa.
Mu Yohane 1:6-7, chinalembedwa kuti, “Kunali munthu, wotumidwa ndi Mulungu, dzina lace ndiye Yohane. Iyeyu anada mwa umboni kudzacita umboni za kuunikaku, kuti onse akakhulupirire mwa iye.” Yohane Mbatizi anabatiza Yesu ndi kupereka machimo onse adziko kwa Iye, kunena kuti, “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” (Yohane 1:29). Tinapulumutsidwa ku machimo athu onse zikomo ku ubatizo wa Yohane pa Yesu Kristu. Kuti Yohane sanabatize Yesu ndi kulankhura kuti Iye anali mwana wa nkhosa wa Mulungu amene anachotsa machimo adziko, sitinakadziwa kuti Yesu anatengera machimo athu onse pa Mtanda. Kapena kudziwa njira yolandiriramo Mzimu Woyera. Koma tithokoze ku umboni wa Yohane, tinamvetsetsa kuti Yesu anachotsa machimo athu onse ndipo tinatha kulandira Mzimu Woyera.
Ndi chikhulupiliro ichi, tinakhala akwatibwi amene ndiwokonzeka kwathunthu kulandira Yesu, mkwati. Ndife anamwali amene amakhulupilira mwa Yesu ndipo ndife okonzeka kwathunthu kulandira Mzimu Woyera.
Kodi mumakhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu Woyera ndi mtima wanu wonse? Kodi mukhulupilira kuti Yesu anachotsa machimo anu onse mwa ubatizo Wake ndi Yohane? Baibulo limati, “Comweco cikhulupiriro cidza ndi mbiri, ndi mbiri idza mwa mau a Kristu” (Aroma 10:17). Tiyenera kukhulupilira kuti Yesu anabatizidwa ndi Yohane ndi kufera pa Mtanda kuti tilandire Mzimu Woyera. Tiyenera kuzindikira kuti kulandira Mzimu Woyera kungathe kubwera kuchokera pokhulupilira kuti Yesu anabwera padziko lapansi ngati munthu ndi kubatizidwa ndi Yohane, komanso kuti Iye anafera pa Mtanda ndi kuukitsidwa kwa akufa.
Ngakhale masiku ano, pali magulu awiri a okhulupilira, monganso m`mene anamwali khumi mu nkhani yapambayi anali m’mitundu iwiri. Kodi inu muli mbali iti? Muyenera kulandira Mzimu Woyera mwakukhulupilira mu madzi ndi Mzimu. Kodi mumapita kukachisi, komabe mumadzipeza kuti mudakali kudikira kuti Mzimu Woyera ubwere kwa inu? Muyenera kudziwa njira yoona yolandiriramo Mzimu Woyera.
Kodi ndi zikhulupiliro ziti zomwe tingalandiriremo Mzimu Woyera. Kodi mungalandire Mzimu Woyera kudzera mu chisangalalo chofunitsitsa zausing’anga? Kodi mungalandire Mzimu Woyera mutakomoka? Kodi mungalandire Mzimu Woyera pakukhulupilira mzipembezo zotentheka? Kodi mufunika kupempherera chikhululukiro cha machimo anu kwa Mulungu mosalekeza? Baibulo linena kuti pamene Yesu anabatizdwa ndi kuturuka m’madzi, Mzimu wa Mulungu unatsika ngati nkhunda. Iye anabatizidwa n’cholinga chakuti anyamule machimo athu onse, ndi kutiuza kuti Iye azapachikidwa kuti alipire mphoto ya zolakwa zathu zonse.
Yesu anabatizidwa ndi Yohane kuti anyamule uchimo wa dziko ndi kupita pa Mtanda kuti tipulumutsidwe ndi kulandira Mzimu Woyera. Ichi ndiye choonadi. Yesu anabatizidwa ndi Yohane, naweruzidwa chifukwa cha machimo athu onse ndi kuuka kwa akufa. Tiyenera kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu kwa Yohane ndi mwazi Wake pa Mtanda kuti tilandire chikhululukiro cha machimo athu. Tingathe kuona kuchokera ku ubatizo wa Yesu (Mateyu 3:13-15) kuti Mzimu Woyera umabwera mwamtendere ngati nkhunda pa iwo a ife amene tayeretsedwa mwakukhulupilira mu ubatizo Wake.
Kuti tilandire Mzimu Woyera, n’chofunikira kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi Yohane ndi mu mwazi Wake pa Mtanda. Mzimu Woyera umadza pa munthu mwamtendere ngati nkhunda pamene wakhulupilira m’chikhululukiro cha chimo. Iwo amene analandira kale Mzimu Woyera ayenera kudziwa ichi chakhala chotheka chifukwa cha chikhululukiro cha uchimo mwachikhulupiliro. Mzimu Woyera umatsikira pa iwo amene akhulupilira m’chikhulupiliro cha uchimo ndi mtima wawo wonse.
Yesu anadza mwa mkate ndi vinyo wa moyo wosatha (Mateyu 26:26-28, Yohane 6:53-56). Pamene Yesu anaturuka m’madzi pambuyo pa ubatizo Wake, kunamveka mau ochokera kumwamba akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera” (Mateyu 3:17).
N’chophweka kukhulupilira mwa Mulungu ngati Mulungu Mtatu. Mulungu ndiye Tate wa Yesu ndipo Yesu ndi Mwana wa Mulungu. Mzimu Woyera nayenso ndi Mulungu. Mulungu Mtatu ndi Mulungu umodzi kwa ife.
Muyenera kudziwa kuti simuzalandira Mzimu Woyera mwakukhulupilira pa Mtanda pokha kapena kuyesera kuziyeretsa nokha ndi machitidwe zolungama. Munagalandire Mzimu Woyera pokhapo mukakhulupilira kuti Yohane anabatiza Yesu kuti aike machimo athu onse pa Iye, ndiponso kuti Iye anapachikidwa kuti atetezere machimo athu. Ndi chophweka komanso chomveka bwino motani choonadi! Sichobvuta kulandira chikhululukiro cha uchimo ndi Mzimu Woyera.
Mulungu analankhula nafe m’njira zosabvuta. Mnzeru za munthu wamba zili pakati pa 110 ndi 120. Uthenga Wake wabwino ndiophweka kwambiri kuti anthu wamba amvetsetse. Ngakhale kwa ana a zaka 4 kapena 5, uthenga wabwino okoma siwobvuta kwa iwo kuti amvetsetse. Koma ngati Mulungu anakalankhula nafe za kukhazikika kwa Mzimu Woyera m’njira yapamwamba, kodi tinakamumvetsa Iye? Mulungu anakhululuka machimo athu mwachilungamo ndi kupereka Mzimu Woyera ngati mphatso kwa iwo amene anakhulupilira mwa uwo.
Mulungu amatiuza kuti sitingalandire Mzimu Woyera kudzera mu kuika manja kapena mapemphero akulapa. Mzimu Woyera siumadza pa chifukwa chosala kudya kapena kudzipereka kapenanso kupemphera usiku wonse kumapiri. Kodi ndi chikhulupiliro chotani mwaife chimene chimapangitsa kulandira Mzimu Woyera? Ndi chikhulupiliro m’choona chakuti Yesu anabwera mdziko lino, anabatizidwa kuti achotse uchimo wathu onse, kufa pa Mtanda, ndi kuukitsidwa.
Kodi tifunikadi kukhulupilira mu ichi?
Kodi chifukwa n’chiani tiyenera kulandira chikhululukiro cha machimo ndipo mwakutero n’kulandila Mzimu Woyera? Kuti tikhale nzika za Ufumu wa Mulungu, tifunika Mzimu Wake. Choncho, kuti tilandire Mzimu Woyera, tifunika kukhulupilira mwa Yesu ngati Mpulumutsi wathu, mu ubatizo Wake ndi mwazi, ndipo potsiriza, tifunika kukhululukidwa ku machimo athu.
Kodi chifukwa n’chiani Mulungu amapatsa Mzimu Woyera ku iwo amene machimo awo anakhululukidwa? Cholinga n’chakuti awaike chizindikiro ngati anthu Ake. Kuti asindikize iwo amene akhululupilira mwa Yesu molingana ndi mawu a Mulungu, Iye amawapatsa Mzimu Woyera ngati chizindikiritso.
Anthu ochuruka kwambiri amasunga mitundu yolakwika ya chikhulupiliro. Ndichophweka kwambiri kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi kulandira Mzimu Woyera. Ndichophweka kwa iwo a ife amene tinalandira kale Mzimu Woyera, koma n’chosatheka kwa iwo amene sanalandire chikhululukiro cha machimo. Iwo sadziwa choonadi ndipo m’malo mwake amafuna funa njira zina zolandiliramo Mzimu Woyera, monga kudzimiza okha mu kukomoka kwa chipembedzo kudzera m’machitidwe otentheka. Iwo ndi ambuli kwambiri moti amasokonezeka ndi mbewu zimene Satana anafesa, ndipo amagwa pansi pa mphamvu ya zipembezo zamizimu.
Mzimu Woyera umakhala mwa iwo amene akhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda ndiponso ndi amene amalandira chikhululuko cha uchimo. Ndi okhawo omwe amakhulupilira m’chipulumutso cha Mulungu amene angabvomereze kuti, “Ine ndiribe tchimo.” Ngati munthu sakhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, ndiyekuti sanganene kuti alibe tchimo. Mofanana, Mulungu anapatsa Mzimu Woyera ngati lonjezo kwa ana Ake amene akhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi pa Mtanda ndiponso alandira chikhululukiro cha uchimo.
Ndi ndani anachitira umboni wakuti ubatizo wa Yesu unachotsa machimo athu onse? Yesu, ophunzira Ake, ndi Mzimu Woyera unachitira umboni zimenezo. Kodi ndidani anakonza zoti apulumutse anthu onse ku machimo awo onse? Ndi Atate Woyera anatero. Kodi ndani anagawira ntchito ya ganizo Lake? Yesu Kristu anatero. Kodi ndindani anatsimikizira kuti ganizoli linachitidwa? Ndi Mzimu Woyera unatero.
Mulungu anafuna kutipanga ife kukhala anthu Ake ndipo mwakutero anaganiza zotipulumutsa ku machimo athu onse kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi. Choncho, Mulungu Mtatu amalonjeza chipulumutso chathu chokwanira ndi kubvomereza chikhululukiro cha machimo athu.
Mu Mateyu 3:17, kwalembedwa, “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.” Iwo omwe ali ndi Mzimu Woyera ndi anthu a Mulungu. Ndi ana Ake. “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.” Yesu ndi Mulungu pachiyambi. Mulungu Atate amatiuza kuti, “Ngati mufuna kulandira chikhululukiro cha machimo anu, khulupilirani kuti machimo onse amunthu anachotsedwa kwa muyaya ndi Yesu, Mwana Wanga wobadwa Yekha, landirani Mzimu Woyera ndi kukhala ana Anga.” Iwo amene amakhupilira mwaizi azalandira chikhululukiro cha machimo awo ndi kukhala ana amuna ndi aakazi a Mulungu. Iye amawapatsa mphatso ya Mzimu Woyera kuti awasindikize ngati ana Ake. Timalandira chikhululukiro cha machimo athu pokhapo tikakhulupilira mu ubatizo wa Yesu pamodzi ndi mwazi.
Ngati anthu satuluka m`mtima zawo ndipo sakhulupilira mu uthenga wabwino wa chikhululukiro, amakhulupilira kuti tchimo la pachiyambi linachoka kale koma kuti ngakhale choncho ayenera kupemphera kosalekeza mapemphero akulapa kuti abweretse chikhululukiro cha machimo awo amasiku onse. Ngati abvutika ndi maganizo otere, Baibulo limakhala losamveka ndiponso losokoneza. Choncho, amakhala ndi zikhulupiliro zosiyana ndi za ophunzira Ake.
Ena amanena kuti Mzimu Woyera umadza pa iwo “kudzera m’mapemphero.” Koma ichi sichoona cheni cheni pakauona zonena za Baibulo. Ichi chingamveke ngati nchomveka, koma Baibulo limanena kuti pamene Yesu anaturuka m’madzi atatha kubatizidwa ndi Yohane, Mzimu Woyera unatsika pa Iye ngati nkhunda. Ichi chitsimikizira kuti ngati tikufuna kulandira Mzimu Woyera, tifunika kukhulupilira kuti Yesu anabwera mdzikoli, anabatizidwa ndi Yohane kuti achotse machimo onse a dziko, anaweruzidwa pa Mtanda mmalo mwa iwo ndi kuukitsidwa kuti akhale Mpulumutsi wathu.
Kodi Mulungu amalankhula chiani kwa ife tikakhulupilira mchoonadi chimenechi ndi kulandira Mzimu Woyera? Iye amati, “Ndiwe mwana wanga. Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera.” Mulungu azalankhula chimodzi modzi kwa iwo amene adzakhulupilira mwa Yesu ndi kukhululukidwa ku machimo awo amtsogolo. Choonadi ichi ndi lonjezo la Mulungu kuti atipange ife kukhala ana Ake.
Koma anthu akuganizabe kuti pali njira zina zolandiriramo Mzimu Woyera. Kodi mukuganiza kuti Mzimu Woyera ungadze kwa inu kudzera mwakulila kwanu ndi mphamvu za padziko? Ntchito za Mulungu zimalamulidwa ndi chifuniro Chake chokha ndipo Iye amapatsa Mzimu Woyera kwa okhawo amene analandira chikhululukiro cha machimo awo. Iye amati, “Ndinapangitsa Mwana Wanga kuti abatizidwe ndi cholinga choti achotse machimo anu onse ndi ndinapangitsa kuti apachikidwe kuti aweruzidwe m’malo mwa iwo. Ndinasankha Mwana Wanga kuti akhale Mpulumutsi wanu. Ngati mubvomera chikhululukiro cha uchimo chimene Mwana Wanga anakwaniritsa, ndiye kuti ndizakutumizirani Mzimu Woyera.”
Atate wathu amachita m`mene Iye akufunira. Ngakhale kuti munthu angagwade usiku wonse ndi kulilira Iye kufikira mapapo ake kutsala pang’ono kuphulika, Mulungu sadzamtumizira kweni kweni Mzimu Woyera. Iye azangomdzudzula, kunena kuti, “Iwe sunabvomerebe nzeru yoona ndipo ukupitiriza kulabadira ku zikhulupiliro zolakwika. Mzimu Woyera uzamanidwa kwa inu ngati mudzapitiriza kukana chikhulupiliro choona.”
Mdziko lino, zisankho za munthu zingasinthe kulingana ndi m`mene zili zinthu, koma lamulo limene Mulungu anapanga lokhululukiramo machimo ndi kupatsa Mzimu Woyera limakhalabe losasinthika. Ngati mwagwera pansi pa tembelero la zikhulupiliro zolakwika, n’chovuta kuti mupezenso njira yoyenera. Baibulo limanena kuti Yesu ndi mwala wopunthwitsa kwa iwo osamvera (1 Petro 2:8).
Anthu amene amakhulupilira mwa Yesu koma sakudziwa chifukwa chimene Iye anabatizidwira amangokhulupilira mutheka lokha la uthenga wabwino wachiombolo ndipo mosakaikila azagwera m’gahena. Nchocho, mukakhulupilira mwa Yesu choyamba, muyenera kudziwa za ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake, m`mene uthenga wabwino wa chikhululukiro cha uchimo umapezeka. Ndipo ngati mwalandira chikhululukiro cha chimo, ndiye kuti muzalandiranso Mzimu Woyera.
Tiyeni tiganizire za moyo wa Yesu padziko lapansi. Yesu anakhala munthu ndipo anachotsa machimo onse adzikoli mwa ubatizo Wake. Iye anafanso pa Mtanda ndi kuweruzidwa cifukwa cha machimo athu kuti atipulumutse kumoto wa Gahena. Iwo amene amakhulupilira mwa iye amalandira Mzimu Woyera ngati mphatso.
Choncho, tonsefe tiyenera kutsatira njira yoyenera kuti tilandire Mzimu Woyera. Chomwe chikufunika ndi kuganiza molingana ndi mau a choonadi. Tikachita ichi, Yesu azakusungani ndi kukudalitsani. Iwo amene amasiya mitima yawo mopanda kanthu ndi kukhulupilira m’mau Ake angakhale m’choonadi polandira chikhululukiro cha uchimo, ndi kutsogoreredwa ndi Mzimu Woyera. Kuonjezerapo, angatsogolere ena m’njira yoyenera ndi thandizo la Mzimu Woyera.
Khulupilirani m’chiombolo chokwaniritsidwa ndi ubatizo wa Yesu komanso mwazi Wake. Ndi pokhapo pamene tingamtsatire ndi chikhulupiliro ndi kulandira dalitso la chikhululukiro cha uchimo, la moyo wamuyaya ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Yesu ndi Mbuye wachikhululukiro, amene anachotsa machimo onse adziko kudzera mu ubatizo Wake ndi imfa pa Mtanda. Yesu anafafaniza machimo athu onse ndi kupereka Mzimu Woyera kwa iwo amene anakhulupilira mu uthenga wabwino wachoonadi. Mungalandire Mzimu Woyera potenga chikhulupiliro choona.