(Yesaya 9:6-7)“Pakuti kwa ife Mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wa mwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lace, ndipo adzamucha dzina lace Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere. Za kuenjenjezera ulamuliro wace, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wacifumu wa Davide, ndi pa ufumu wace, kuukhazikitsa, ndi kuucirikiza ndi ciweruziro ndi cilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Cangu ca Yehova wa makamu cidzacita zimenezi.”
Kodi n’chiyani chimalola Mzimu Woyera kukhala mwa okhulupirika?
Uthenga Wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu
Kuti tilandire Mzimu Woyera, tiyenera kukhala ndi chikhulupiliro mu uthenga wa madzi ndi Mzimu. Ambuye athu akutchedwa Wodabwitsa, Wauphungu, ndiponso Mulungu Wamphamvu. Mulungu wathu anaziyerekezera Yekha ngati njira ya Kumwamba. Yesu Kristu anapereka kwa aliyense mphatso ya uthenga wabwino okoma.
Komabe, m’dzikoli, muli anthu ambiri amene akukhalabe mu mdima. Amayesa kuthawa ku mdima umenewu koma chifukwa sakudziwa za uthenga wabwino okoma, sangayese kuthawa ku machimo awo. M’malo mwake amauma ku chikhulupiliro chawo cha mu ziphunzitso zabodza. Mosemphana, kwa iwo amene amafuna choonadi, adzapeza uthenga wabwino okoma ndi kukhala ndi umoyo wawo onse odzala ndi madalitso a Mulungu. Ndikhulupilira kuti ndi madalitso apadera a Mulungu amene amalola ine kuti ndiwathandize kupeza uthenga wabwino okoma ndi kuwayeretsa ku machimo awo.
Choncho, kumasuka ku uchimo kukanakhala kosatheka ngati sikunali kwa dalitso Lake. Ngati takumana ndi Ambuye ndi kulandira Mzimu Woyera ndiye kuti ndife odalitsika kwambiri. Zachisoni, anthu ambiri sakudziwa kuti madalitso a Mulungu amabwera kuchokera ku chikhulupiliro cha mu uthenga wabwino okoma umenewu.
Madalitso a Mulungu amachokera mu kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma umene unapatsidwa ndi Yesu Kristu, Mwana Wake obadwa yekha. Yesu ndi amene amatipulumutsa ife ku machimo adziko ndi kutidalitsa ndi chifundo Chake. Palibe amene angatipulumutse kumachimo kapena kutithandiza kufufuta mlandu mu mitima yathu. Kodi ndani akanatha kuzipulumutsa yekha ku machimo ake ndi chowawa cha imfa yosatha?
Mulungu amatiuza kuti, “Iripo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka, koma matsiriziro yace ndi njira za imfa” (Miyambo 16:25). Anthu amakhazikitsa zipembezo zawo ndi kuzipereka okha ku chionongeko ndi imfa. Zipembezo zambiri zimazikuza kuti zimanena zachilungamo ndi kuonetsa njira zawo za kupulumutsira anthu ku machimo awo koma ndi uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu okha, umene Ambuye wathu anapereka kwa ife, umene ungatipulumutse ku machimo athu onse. Ndi Yesu yekha amene ndi Mpulumutsi amene angapulumutse ochimwa kumachimo awo.
Mu Yohane 14:6, Ambuye wathu anati, “Ine ndine njira, ndi coonadi, ndi moyo.” Iye anapereka thupi lake ndi mwazi kwa iwo amene ali pa njira ya kuimfa. Iye anaziyerekezanso Yekha ngati njira ya ku umoyo oona. Mulungu amanena kuti ngati munthu sakhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa Yesu, sangalowe mu Ufumu wa Kumwamba.
Tiyenera kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, tikhululukidwe machimo athu ndi kukhulupilira kuti Iye ndi Mpulumutsi kuti tikalowe mu Ufumu wa Kumwamba.
Nthawi Ina mu Israyeli Wakale!
“Ndipo panali masiku a Ahazi, mwana wa Yotamu, mwana wa Uziya, mfumu ya Yuda, kuti Rezini, mfumu ya Aramu, ndi Peka, mwana wa Remaliya, mfumu ya Israyeli, anakwera kunka ku Yerusalemu, kumenyana nao; koma sanathe kupambana” (Yesaya 7:1).
Israyeli linali dziko limodzi. Komabe, Israyeli anagawanika kukhala kumwera ndi kumpoto. Kachisi wa Mulungu anali ku Yerusalemu kumwera kwa Yudeya, kumene Rehabiamu, mwana wa mfumu Solomo, anali kulamulira. Patapita nthawi, Yerobiamu, m’modzi wa akapolo a Solomo, anakhazikitsa dziko lina kumpoto ndipo motero Israyeli anagawanikana. Kuchokera pa nthawi imeneyo, chikhulupiliro mwa Mulungu chinatha. Kutha kwa chikhulupiliro kunakhala kuyamba kwa zipembezo zatsopano zampatuko. Yerobiamu anakhala mwini wa ampatuko. Iye anasintha lamulo la Mulungu chifukwa anali kufuna kusunga ufumu wake ndipo motero, anakhala atate wa ampatuko. Iye analenga chipembedzo chosiyana cha anthu ake mu Israyeli, Ufumu wa Kumpoto ndipo anafuna ngakhale kulanda Yuda, Ufumu wa Kumwera. Pafupifupi zaka 200 zinatha, koma ubale wabwino pakati pa maufumu awiriwa unali osasinthika.
Koma, Mulungu anayankhula kudzera mwa Yesaya, “Cifukwa Aramu ndi Efraimu, ndi mwana wa Remaliya anapangana kukucitira zoipa, nati, tiyeni, tikwere, timenyane ndi Yuda, timbvute; tiyeni, tidzigumulire mpata, pamenepo tikhazike mfumu pakati pace, ngakhale mwana wamwamuna wa Tabeeli; athero Ambuye Yehova, Upo wao sudzaimai, sudzacitidwa. Pakuti mutu wa Aramu ndi Damasiko, ndi wa Damasiko ndi Rezini, zisadapite zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu zisanu Efraimu adzatyokatyoka, sadzakhalanso mtundu wa anthu; ndipo mutu wa Efraimu ndi Samariya, ndi mutu wa Samariya ndi mwana wa Remaliya, mukapanda kukhulupirira ndithu simudzakhazikika” (Yesaya 7:5-9).
Pa nthawi imeneyo, Mulungu ananenera kudzera mwa Yesaya kwa mfumu Ahazi, koma mfumu inalibe chikhulupiliro mwa Iye. Ahazi anali odankhawa kuti sangakwanitse ngakhale kulimbana ndi kuukirana ndi asilikali a ku Siriya, koma pakumva za nkhondo ya Siriya ndi Israyeli pogwirizana wina ndi mnzake, ananjenjemera mwamantha. Koma kapolo wa Mulungu, Yesaya, anabwera ndi kumuuza kuti, “Mu zaka zochepekera makumi asanau ndi limodzi kudza mphambu zisanu, Israyeli wakumpoto uzaonongedwa. Ndipo chiwembu choipa chimene mafumu awiriwa anabweretsa sichizakhala choona.”
Kapolo wa Mulungu anauza Ahazi kuti afune chizindikiro kwa Mulungu. “Udzipemphere wekha cizindikilo ca kwa Yehova Mulungu wako; pempha cam’mwakuya, kapena cam’mwamba” (Yesaya 7:11). “Mverani inu tsopano, inu a nyumba ya Davide; kodi ndi kanthu kakang’ono kwa inu kutopetsa anthu; kuti inu mutopetsa Mulungu wanga? Cifukwa cace Ambuye mwini yekha adzakupatsani inu cizindikilo; taonani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, nadzamucha dzina lace Imanueli.” (Yesaya 7:13-14). Uwu unali uneneri Wake: Kuti adzapulumutsa anthu Ake ku machimo Awo.
Kodi mdani wa Mulungu ndindani?
Mdani wa anthu ndi uchimo ndipo uchimo umachokera kwa Satana. Ndipo kodi Mpulumutsi ku machimo athu ndi ndani? Mpulumutsi siwina koposa Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu. Munthu ali ndi zofoka zachikhalile zathupi ndipo motero sangathe koma kuchita tchimo. Iye ali pansi pa mphamvu ya Satana. Anthu ambiri akulu akumapitabe kwa olosera ndi kuyesa kukhala ndi moyo wawo monga aneneri onyengawa akuwalangizira. Uwu ndi umboni oonekeratu kuti ali pansi pa ulamuliro wa Satana.
Ambuye anapatsa Yesaya chitsimikizo cha chipulumutso, pamene ananena kuti namwali adzabala Mwana wamwamuna ndipo adzamutcha Iye Emanueli. Chinali chikonzero cha Mulungu kuti atumize Yesu mchifanizo cha thupi lauchimo la munthu ndi kulola Iye kuti apulumutse ochimwa ku nkhanza za Satana. Mogwirizana ndi uneneri, Yesu anabwera m’dzikoli ngati munthu obadwa mwa namwali Mariya.
Kukanakhala kuti Yesu sanabwere kwa ife, tikanakhalabe pansi pa ulamuliro wa Satana kufikira tsopano. Koma Yesu anabwera m’dziko lino ndipo anabatizidwa ndi Yohane ndi kufa pa Mtanda pofuna kutipatsa ife uthenga wabwino okoma umene udzapulumutsa ochimwa onse kumachimo awo. Choncho, anthu ambiri anakhulupilira mu uthenga wabwino okoma, analandira chikhululukiro cha machimo awo ndipo anakhala ana a Mulungu.
Ngakhale masiku ano, a zaumulungu ambiri amatsutsa kuti kaya Yesu Kristu ndi Mulungu kapena munthu. A zaumulungu akale amenewa amanena kuti, “Yesu ndi Mulungu, koma a Zaumulungu ena Atsopano amayankha potsutsa kunena kuti Yesu anali mwana wapathengo wa Yosefe. Kodi ndi mawu olilitsa chotani amenewa!
Azaumulungu ena atsopano amanena kuti sangakhulupilire kuti Yesu anali ndi kuthekera koyenda pa madzi. Iwo amanena kuti, “Yesu anayenda pa phiri la pansi la mphepete ndipo ophunzira Ake, atamuona patali anaganiza kuti anali kuyenda pamadzi.” Adotolo amasiku-ano a azaumulungu amene ndi a pamasukulu a Zaumulungu Atsopano sionse amene ali akulu mu zaumulungu. Ambiri a iwo amasankha kukhulupilira zimene angazimvetsetse mu Baibulo zokha.
Kupereka chitsanzo china, Baibulo limanena kuti Yesu anadyetsa anthu 5,000 ndi nsomba ziwiri ndi mikate isanu. Koma anakhalabe okayikira pa za chozidzitswachi. Amafotokoza mu mawu otsatirawa. “Anthu amene anali kutsatira Yesu anali kuzunzika mpaka kufa. Choncho Yesu anauza ophunzira Ake kuti asonkhanitse zakudya zotsala. Ndiyeno mwana anamupatsa chakudya chake mozifunira, ndi ena onse akuluakulu anakhudzidwa ndi kutenga zakudya zawo. Choncho atasonkhanitsa zakudya zonse ndi kudya, madengu khumi limodzi ndi awiri anatsala.” A zaumulungu otere amayesa kupanga mawu a Mulungu kuti akhale m’mene iwo akuwamvelera.
Kukhulupilira mu choonadi cha Mulungu ndi kukhala ndi chikhulupiliro mu uthenga wabwino okoma umene Mulungu anapereka. Chikhulupiliro sichitanthauza kukhulupilira chinthu chimodzi chokha chifukwa chakuti chikuoneka kuti chikupanga nzeru kapena kulephera kukhulupilira mu chinthu china chifukwa sichikutero. Kaya tikudziwa kapena ai, tiyenera kukhulupilira Iye ndi kuvomera mawu Ake monga analembedwera.
Choona chakuti Yesu anadza kwa ife ngati Mwana wa Munthu chikutanthauza kuti anatumidwa kudzatipulumutsa ku machimo athu. Yesu, amene ndi Mulungu, anabwera padzikoli kudzatipulumutsa ife. Yesaya ananenera kuti adzabwera kwa ife ngati Mwana wa Munthu, obadwa mwa namwali.
Mu Genesis 3:15, Ambuye Mulungu anati kwa njoka, “Ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yace; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira citende cace” Ichi chikutanthauza Mulungu anakonza kale kutumiza Yesu, m’maonekedwe monga a munthu, ngati Mpulumutsi wathu kuzapulumutsa mtundu wa anthu ku machimo awo.
Mu Baibulo, munalembedwa kuti, “Imfawe, cigonjetso cako ciri kuti? Imfawe, mbola yako iri kuti? Koma mbola ya imfa ndiye ucimo; koma mphamvu ya ucimo ndiyo cilamulo” (1 Akorinto 15:55-56). Mbola ya imfa ndi uchimo. Pamene munthu wachimwa, imfa imamupangitsa kukhala kapolo. Koma Ambuye wathu anatilonjeza, “Mbeu ya mkazi idzaphwanya mutu wako.” Ichi chikutanthauza kuti Yesu adzaononga mbola ya uchimo imene Satana anabweretsa.
Yesu anabwera m’dzikoli, anabatizidwa kuti achotse machimo onse adziko ndipo anapachikidwa ndi kuweruzidwa chifukwa cha iwo. Anapulumutsidwa kumachimo awo onse iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma. Pamene Adamu ndi Hava anachimwa, Mulungu analonejza kupulumutsa mtundu wa anthu ku mphamvu za Satana. M’dziko latsopano, mdani wa Mulungu ndi iwo amene sakhulupilira mu uthenga wabwino okoma.
Kodi chifukwa n’chiyani Yesu anabadwa m’dziko lino?
Mulungu anatipatsa lamulo ndi uthenga wabwino okoma kuti atipulumutse kumachimo athu. Pansi pa lamulo la Mulungu, anthu anakhala ochimwa pamaso Pake. Chimodzimodzi, lamulo linaperekedwa ndi cholinga choti anthu adziwe machimo awo. Pamene anthu anakhala akapolo a uchimo ndi kulamulo, Ambuye wathu anadza m’dziko lino kuzakwaniritsa chilungamo cha zofunikira za lamulo.
Yesu anabadwa pansi pa lamulo. Iye anabadwa m’nthawi ya lamulo. Chifukwa chimene anthu ayenera lamulo chinali chakuti anafunika kudziwa machimo awo pofuna kuti alandire chikhululukiro cha iwo. Anthu amayeretsa litsiro la ku zovala zawo pokhapo ngati azindikira litsiro lake. Chimodzimodzi, kuti azindikire machimo awo, anthu ayenera kudziwa lamulo la Mulungu. Kukanakhala kuti kunalibe lamulo, kukanakhala kulibe nzeru ya machimo, ndipo Yesu sakanayenera kubwera padziko lino.
Ngati mukudziwa lamulo la Mulungu, ndiye kuti muli ndi mwayi okumana ndi Iye. Tinadziwa za lamulo ndipo motero tinatha kuphunzira za machimo athu. Pokhapo pamene tinadziwa za uchimo wathu ndi pamene Yesu Kristu anabweretsa uthenga wabwino okoma kwa ife kuti tiukhulupilire. Kukanakhala kuti Mulungu sanatipatse lamulo, ndiye kuti sitikanakhala ochimwa ndipo chiweruzo sichikanakhalako. Motero, Mulungu anatipatsa lamulo ndi kutionetsa uthenga wabwino okoma kupulumutsa ochimwa onse ku machimo awo.
lamulo limene liyenera kukhalapo pakati pa Mlengi ndi zolengedwa zake ndi lamulo la Mulungu la chipulumutso. Ili ndi lamulo la chikondi. Mulungu anauza munthu, “Koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo” (Genesis 2:17). Ili ndi lamulo Mulungu anapereka kwa ife, ndipo lamulo linakhala kuchimake kwa chikondi kumene Mulungu anatipulumutsira ife tonse ku machimo athu. Lamulo la chipulumutso linali ndi maziko ake mu chikhululukiro cha machimo athu. Mulungu amatiuza kuti Iye ndi Mlengi wathu ndiponso kuti zonse zinakhalako mogwirizana ndi chifuniro Chake. Ichi chikutanthauza kuti Mulungu ndi Wakukhalako Weniweni ndipo kuti anthu ayenera kukhulupilira mu lamulo la chipulumutso limene linakwaniritsidwa kudzera mu uthenga wabwino okoma.
Mulungu Weniweni ndi wabwino kwathunthu. Chikondi cha Mulungu ku dziko lino chinapangitsa Iye kupereka nsembe Mwana Wake, amene anadzakhala Mpulumutsi wa ochimwa onse. Kukanakhala kuti Mulungu anatilenga ndipo sanatipatse uthenga wabwino Wake okoma kuti apulumutse ife ku machimo athu, tikanadandaula kwa Iye. Koma Mulungu anafuna kutipulumutsa ku chionongeko chathu ndipo motero anakhazikitsa lamulo la chipulumutso. Chifukwa cha lamulo, tinatha kuzindikira machimo athu ndipo mwa kuwayangira bwino, tinayamba kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa Yesu. Pamene tikuononga mawu a Mulungu, timaonedwa ngati ochimwa pamaso pa lamulo, ndipo pakutha pa zonse ife ochimwa timagwada pansi kupempha chifundo Chake cha chikhululukiro cha uchimo pamaso pa Mulungu.
Yesu anabadwa kwa mkazi ndipo anabwera padzikoli kudzapulumutsa mtundu wa anthu ku uchimo. Yesu anabwera padzikoli ngati munthu kuzakwaniritsa chikonzero cha Mulungu kwa ife. Timakhulupilira mu uthenga Wake wabwino okoma. Motero, timatamanda Ambuye.
Ena amadandaula, “N’chifukwa chiani Mulungu anapanga ine ofoka chotere mwakuti ndimagwera mu uchimo mosavuta ndipo ndavutika kwambiri chifukwa cha zolakwa zanga?” Koma Mulungu sanafune kuti ife tizivutika. Iye analola kuti ife tivutike chifukwa tinali osakhulupilira uthenga wabwino wa Yesu. Mulungu anatipatsa kuvutika ndi uthenga wabwino okoma pofuna kuti tikhale ndi mphamvu zimodzi monga Iye ngati ana Ake. Ichi chinali chikonzero Chake.
Koma ziwanda zimanena kuti, “Ai! Ai! Mulungu ndiye olamulira! Pitirizani ndi kukhala m’mene mukufunira, Khalani panokha! Pangani mwayi wanu kudzera mu mphamvu zanu!” Ziwanda zimafunanso kutchingira mtundu wa anthu kukhulupilira mwa Mulungu. Koma iwo amene amasankha kukhala kutali ndi Mulungu ndi zotchinga za chikonzero Chake cha chipulumutso. Yesu anabwera m’dzikoli ndi kuitana iwo amene ali pansi pa mphamvu ya Satana kuti aleke machimo awo. Sitiyenera kukhala kutali ndi Mulungu.
Munthu amabadwa ochimwa amene ali oyenera ku Gahena
Palibe choonadi padziko lapansi chimene sichimasintha. Koma uthenga wabwino okoma wa Yesu ndi choonadi chosasinthika. Motero, anthu angadalire choonadicho ndi kuomboledwa ku mphamvu ya satana. Mtundu wa anthu unatenga machimo a Adamu ndi Hava ndipo kopanda kulowerera kwa Kristu tikanapita ku moto wa Gehena. M’malo mwake, zikomo chifukwa cha nsembe Yake, munthu anadalitsidwa ndi mphamvu yokhala mwana wa Mulungu. “Koma kumene kuli nsautso sikudzakhala kuziya” (Yesaya 9:1). Mulungu anatumiza Mwana Wake padzikoli ndi kulemekeza iwo amene amakhulupilira mu chipulumutso chokoma.
“Anthu amene anayenda mumdima, anaona kuwala kwakukuru; iwo amene anakhala m’dziko la mthunzi wa imfa, kuwala kwaturukira kwa iwo” (Yesaya 9:2). Lero, mawu amenewa akwaniritsidwa kwa inu ndi ine. Mwa kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma, tinadalitsidwa ndi moyo osatha, umene sitingakhale nawo padziko lino. Yesu Kristu anapulumutsa mtundu wa anthu ku machimo onse adziko ndiponso kwa iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma, Iye anapereka moyo osatha ndi Ufumu wa Kumwamba.
Iye anawalitsa kuunika kokoma kwa uthenga wabwino pa iwo amene analibe chiyembekezo
Munthu, ngati mame, amapezeka m’dziko lino kwa kanthawi koma amasowa mwamsanga. Moyo wake uli ngati uja wa zomera ndi udzu wa pa chaka. Udzu umabweretsa moyo wake wamphamvu kwa miyezi yochepa yokha m’chaka ndi kusowa malingana ndi chitetezero cha Mulungu. Zonse ndi zachabe mu miyoyo yathu ndipo ndi zopanda tanthauzo monga udzu uwu. Koma Mulungu anapereka uthenga wabwino okoma ku miyoyo yathu yotopa ndipo ndi chilungamo Chake, anapanga ife kukhala ana Ake. Kodi ndi chisomo chodabwitsa motani chimenechi! Miyoyo yathu yopanda tanthauzo inakhala miyoyo yamuyaya tikuthokoza chikondi cha Mulungu ndipo tinadalitsidwanso ndi ufulu okhala ana Ake.
Pano pali kuvomereza kwa moyo umene unadalitsidwa ndi chisomo cha Mulungu pokhulupilira mu uthenga wabwino okoma umenewu.
“Ndinabadwa mu banja limene silinali kukhulupilira mwa Mulungu. Motero, ndinkakula ndi kuganizira kuti ndikwabwino kuti amai anga azipemphera kwa milungu ya kumwamba ndi ya padziko kuti banja lathu likhale labwino m’mawa ulimonse ndi mbale ya madzi patsogolo pawo. Pamene ndinali kukula, sindinali kudziwa za kufunikira kwanga kapena chifukwa cha kukhalako kwanga, chimene chinapangitsa ine kuti ndikhulupilire kuti zinalibedi kanthu kuti kaya ndizikhala kapena kufa. Chifukwa sindinali kudziwa za kufunikira kwanga, ndinali kukhala ndekha.
Moyo otere unanditopetsa ndipo ndinathamangira kukwatira. Moyo wanga wa ukwati unali wabwino. Ndinalibe chilichonse chimene ndinkakhumba, choncho ndikhala moyo wodekha ndiponso moyo wamtendere. Ndipo kenako ndinakhala ndi mwana ndipo kuyambira nthawi imeneyo ndinapeza kuti chikondi chinayamba kuoneka mwa ine. Ndinayamba kutaya zokhumba zanga zozikonda koma ndinaoponso kutaya kwa iwo amene anali nane pafupi.
Motero, ndinayamba kufunafuna Mulungu. Ndinali ofoka ndiponso olephera ndipo motero, ndinafunika Wakukhalako Weniweni kuti aziyang’anira okondedwa anga. Choncho ndinayamba kupezeka ku mpingo koma chikhulupiliro changa chinali chosiyanako ndi cha amai anga popeza anali kupemphera kutsogolo kwa mbale ya madzi ─ mapemphero anga anali oimilira pa mantha osamveka ndi pa ziyembekezo.
Tsiku lina ndinapezeke pa msonkhano wina waung’ono omwe unachitikira pa mpingo wamba ndipo pamene ndinali kupemphera, misozi inayamba kugwa kuchoka m’maso mwanga. Ndinachita manyazi ndipo ndinayesa kuleka kulira, koma misozi inapitiriza kugwa. Anthu omwe anali pafupi nane anaika manja awo pa mutu panga ndi kundiyamikira polandira Mzimu Woyera. Koma ndinali osokonezeka maganizo. Sindinali ngakhale odziwa mawu a Mulungu ndipo chikhulupiliro changa mwa Iye chinali chosamveka konse, Choncho ndinalibe chitsimikizo kuti mphamvuyi inali ya Mzimu Woyera.
Mpingo umene ndinali kupezekako unali ogwirizana ndi Kayendetsedwe ka kutentheka kwa Chipentekosite, ndipo ambiri anaona m’mene ndinali kuonera ndipo pafupifupi aliyense anali kulankhula m’malilime. Tsiku lina, ndinaitanidwa ku msonkhano wachitsitsimutso otsogoleredwa ndi mbusa yemwe anthu anali kunena kuti anadzadzidwa ndi Mzimu Woyera. Mbusa anasonkhanitsa anthu ambiri ku mpingo ndi kunena kuti angachiritse chimfine cha munthu ndi kukhala m’mene analili popeza ndi mphamvu yake ya Uzimu kuchita choncho. Komabe, ndinaganizira kuti chimfine chinali nthenda imene ikanachiritsidwa kuchipatala mosavuta, choncho ndinali osangalatsidwa m’mene iye analandilira Mzimu Woyera. Koma pamene mbusa anaoneka kuti akuchita bwino pakuyesa kuchiritsa, anayamba kuzitukumula kuti angalosere kuti kaya mwana wa sukulu yapamwamba angachite bwino mu mayeso ake opitira ku yunivesite kapena ai. Anthu ambiri anatamanda mphamvu zake ngati kuti zinali za Mulungu.
Koma sindinamumvetse iye. Ndipo sindinanene kuti mphamvu zilizonse zimene mbusayo anali nazo, zilibe ntchito ndi Mzimu Woyera. Sindinaganizire kuti kunali koyenera kaya angachiritse chimfine kapena kulosera za kupambana kwa munthu wina pa mayeso. Choncho, sindinatenge zodabwitsa zake ngati ntchito za Mzimu Woyera.
Mphamvu ndi chikondi cha Mulungu chimene ndinali nacho m’maganizo mwanga chinali chosiyana ndi zimene ndinaona. Pa chifukwa chimenecho, ndinasiya kupezeka ku mpingo umenewo ndipo ndinali kupewa anthu amene anali kukhulupilira mwa mphamvu za mbusayo. Kuchoka pamenepo, ndinapezeka pa mpingo wodekha, umene ndinasankha chifukwa ndinali kukhulupilira kuti unali kunena kwambiri za mawu a Mulungu. Ndinaphunzira za lamulo ndipo kudzera mwa ilo ndinali osalungama. Mulungu anakhala chikhazikitso cha mantha anga ndipo ndinaphunzira kuti sindiyenera kuoneka olemekezeka pamaso Pake ndipo kuti Mzimu Wake unaoneka ngati ukundikana.
Mu Yesaya 59:1-2 munalembedwa kuti, “Taonani, mkono wa Yehova sufupika, kuti sungathe kupulumutsa; khutu lace siliri logontha, kuti silingamve; koma zoipa zanu zakulekanitsani inu ndi Mulungu wanu; ndipo macimo anu abisa nkhope yace kwa inu, kuti Iye sakumva” Ichi chinaoneka ngati chinagwirizana ndi m’mene ndilili. Kunali kosatheka kwa ine kukhala mwana Wake ndi kulandira Mzimu Woyera chifukwa zilizonse zomwe ndinkachita kapena kuganiza zinali zauchimo.
Ndinali kuopa Mulungu choncho ndinali kulimbikira kupemphera mapemphero akulapa. Palibe yemwe anandiuza kuchita choncho, koma ndinali kufuna kuima molemekezeka pamaso pa Mulungu. Chifukwa ndinali ochimwa, ndinali kupemphera molimbika ngakhale mapemphero a kulapa. Koma mapemphero amenewa analephera kutsuka machimo anga. Zonse zimene ndinkachita ndi kuonetsa Iye maganizo anga ndi kukhulupirika kwanga choncho machimo anga anali adakali mwa ine. Kuchokera pa nthawi imeneyo, ndinayamba kupereka madandaulo kwa Mulungu. Ndinali kufuna kukhala wangwiro pamaso Pake koma sindinakhale wangwiro pomwepo, choncho madandaulo anga ndi machimo anachuruka.
Panthawi imeneyi ya kusokonezeka kwa chipembezo, atate anga anali ndi matenda akufa ziwalo. Anavutika kwa masiku 40 mu chipinda chochotsera ziwalo ndi m’mabedi a kuchipatala asanamwalire. Koma sindinathe kupempherera atate anga. Ndinali ochimwa, choncho ndinaganiza kuti ngati ndingapempherere atate anga, zowawa zawo zizakhaliratu zochuruka. Ndinali okwiya chifukwa chakupanda mwayi wa chikhulupiliro ndipo ndinafuna kutsatira Mulungu koma sindinachite choncho, motero ndinapitiliza kudandaula ndipo pothera pake ndinachoka kwa Iye. Moyo wanga wachipembezo unatha choncho. Ndinaganiza kuti ndikakhulupilira mwa Iye, Mzimu Wake udzakhala mwa ine ndipo ndidzapeza mtendere, koma umu si m’mene zinalili. Kuchoka apo, moyo wanga unakhaliratu opanda tanthauzo ndipo ndinali kukhala mu mantha ndiponso osakondwa.
Koma Ambuye sanandisiye. Iye anapangitsa kuti ndikumane ndi okhulupilira amene analandiladi Mzimu Woyera kudzera m’mawu a Mulungu. Ndinaphunzira kuchokera kwa munthu ameneyu kuti Yesu ananyamula machimo athu kudzera mu ubatizo Wake ndi Yohane ndi kuti anaweruzidwa chifukwa cha iwo pa Mtanda. Choncho, machimo onse adziko lino, kuphatikizapo anga, onse anakhululukidwa. Pamene ndinamvera ndi kumvetsetsa chimenechi, ndinaona kuti machimo anga onse anayeretsedwa. Mulungu anandithandiza kulandira chikhululukiro cha machimo anga, anandipatsa madalitso Mzimu Woyera ndi kundipatsanso moyo wamtendere. Iye modekha ananditsogolera, kundipatsa kamvetsetsedwe komveka bwino ka chabwino ndi choipa ndi kundipatsa mphatso ya mphamvu ya kugonjetsa mayesero onse a dziko lino. Iye anayankha mapemphero anga ndi kundithandiza kukhala olungama ndiponso moyo woyenerera. Ndikuyamika moona Mulungu pakundipatsa Mzimu Woyera.”
Aliyense wa ife ndi odalitsika ndi chisomo cha Mulungu ndipo ndi oyenera kulandira Mzimu Woyera. Ndikuyamika Ambuye pakutipatsa uthenga wabwino okoma. Mulungu anadalitsa olungama ndi chikondwerero chotere. Mitima ya olungama ndi yachimwemwe. Ambuye anatipatsa chikondwerero chamuyaya. Tikudziwa m’mene chipulumutso cha Mulungu, chikondi ndiponso chisomo chilili chamtengo wapatali ndipo ndife othokoza chifukwa cha zimenezo. Ambuye anatipatsa chikondwerero kudzera mu uthenga wabwino okoma wa Kumwamba. Ichi ndi chinthu chimene sichingagulidwe ndi ndalama. Mulungu anatitumizira Mzimu Woyera ndiponso uthenga wabwino okoma pofuna kutipanga kukhala okondwa ndiponso oongoka. Uthenga wabwino okoma ndi umene umapangitsa miyoyo yathu kudalitsidwa. Ambuye anatipatsa uthenga wabwino okoma ndipo ndi okondwera kuti olungama akusangalala ndi moyo odalitsika.
Monga analembera mu Luka, Mariya anati, “Cifukwa palibe mau amodzi akucokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu…Onani, mdzakazi wa Ambuye; kukhale kwa ine monga mwa mau anu” (Luka 1:37-38). Panthawi imene Mariya anakhulupilira mu mawu okongola a Mulungu, monga kunalankhulidwa ndi mngelo Wake, Yesu anabadwa. Chimodzimodzi, kudzera mu chikhulupiliro chawo, olungama amabala uthenga wabwino okoma m’mitima yawo.
“Pakuti gori la katundu wace, ndi mkunkhu wa paphewa pace, ndodo ya womsautsa, inu mwazityola monga tsiku la Midyani” (Yesaya 9:4). Satana anapangitsa mavuto onse, matenda, ndiponso chowawa m’miyoyo yathu koma ndife ofoka kutali kuti timugonjetse. Koma Mulungu amatikonda ndipo motero anamenyena ndi Satana ndipo anamugonjetsa.
“Pakuti kwa ife Mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wa mwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lace, ndipo adzamucha dzina lace Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere. Za kuenjenjezera ulamuliro wace, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wacifumu wa Davide, ndi pa ufumu wace, kuukhazikitsa, ndi kuucirikiza ndi ciweruziro ndi cilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Cangu ca Yehova wa makamu cidzacita zimenezi.” (Yesaya 9:6-7).
Mulungu analonjeza kuti adzatipatsa ulemerero ngati ana Ake kudzera mu uthenga wabwino okoma umene Yesu anabweretsa. Iye anagonjetsa Satana mogwirizana ndi lonjezo Lake ndi kutiombola ife ku mphamvu za Satana.
Ambuye anabwera padziko lapansi ndipo ndi mphamvu Zake analonjeza kudzachotsa mdima onse wa uchimo. Choncho tikuitananso Ambuye wathu kuti Iye ndi Wodabwitsa. Iye wachita zinthu zambiri zodabwitsa kwa ife. Ganizo la Mulungu lobwera padziko lapansi ngati Mwana wa munthu linali lodabwitsa. Ambuye anati, “Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu ziri zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale ziri zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbu” (Yesaya 1:18).
Ambuye analonjeza kutipulumutsa ku machimo athu ndi kutipatsa chikhululukiro chamuyaya. Yesu akuyerekezedwa ngati Iye Wodabwitsa ndipo, moyenerera, anachita ntchito zodabwitsa za ife. “Dzina lace Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu” Mulungu, monga, Wauphungu wathu, anakonza chipulumutso chathu mwa uthenga wabwino okoma ndipo anakwaniritsa chikonzero Chake kutipulumutsa kwamuyaya ku machimo athu.
Kupusa kwa Mulungu ndi kwa nzeru koposa munthu. Zinali nzeru Zake kuti Yesu abatizidwe ndi Yohane ndi kufa pa Mtanda pofuna kuti atipulumutse ku machimo athu onse. Iyi ndi ntchito yodabwitsa imene anachita kwa ife, koma ndi lamulo la chikondi chimene chinatipulumutsa ife ku machimo athu onse. Lamulo la chikondi ndi uthenga wabwino wa choonadi umene umatitengera kukalandira Mzimu Woyera kudzera m’madzi ndi mu mwazi Wake.
Ambuye anati mu Yesaya 53:10, “Koma kunakomera Yehova kumtundudza; anammvetsa zowawa.” Yesu anapeka moyo Wake nsembe ya uchimo kotero kuti achite chifuniro cha Mulungu. Iye anapereka machimo adziko kwa Mwana Wake, Yesu Kristu, ndipo anamulola kuzunzika chowawa cha kupachikidwa kotero kuti aweruzidwe chifukwa cha iwo. Uwu ndi uthenga wabwino okoma umene unapulumutsa anthu ku machimo awo kamodzi kokha. Khristu anapereka moyo Wake chifukwa cha ife, analipira mphoto ya uchimo ndi kutidalitsa ndi chipulumutso.
Ndondomeko ya kaperedwe ka nsembe ya Mulungu
Kodi ndi machimo angati?
amene Yesu anatenga kudzera mu ubatizo Wake ndi Yohane Machimo akale, atsopano ndi amtsogolo kuyambira nthawi yoyamba kufikira yomaliza
Baibulo limanena za nsembe imene inakhala chikhululukiro cha machimo a patsiku. Ochimwa anali kuyenera kubweretsa nyama yopanda chilema ndi kuika manja ake pa mutu pa nyamayo kuti apereke machimo ake. Kenako anayenera kupha nsembe ndi kupereka mwazi wake kwa wansembe. Ndipo wansembe anali kutenga mwazi ena a nyama ndi kuika pa miyanga ya pa guwa la nsembe zopsereza ndi kuthira yotsarirayo pansi pa guwa.
Mwa njira imeneyi, akanapulumutsidwe ku machimo a tsiku limodzi. Kuika manja inali njira ya ochimwa kupereka machimo ake pa nsembe. Iwo amene anali kupereka nsembe zawo mogwirizana ndi mwambo wa kaperekedwe ka nsembe ankalandira chikhululukiro cha machimo awo. Mwambo wa kuperekera nsembe unali njira imene tinkatetezera machimo athu panthawi imene Yesu asanachotse machimo athu onse.
Mulungu anaikanso Tsiku Lotetezera machimo ndicholinga choti anthu a ku Israyeli apange chitetezero cha machimo amene anachita kwa chaka chonse. Mwambo wansembe unali kuchitikira pa tsiku la khumi la mwezi wachisanu ndi iwiri. Mulungu anasankha Aroni, mkulu wansembe, amene adzapereke machimo a pa chaka a Israyeli onse pa mbuzi yamoyo. Mwambo unali kuchitika mogwirizana ndi chikonzero cha Mulungu. Chikululukiro cha machimo chinachokera ku nzeru Yake ndi chikondi cha mtundu wa anthu. Iyi ndi mphamvu Yake.
“Nyanga za pa guwa la nsembe yopsereza” zikuimira “Mabuku Achiweruzo” (Chivumbulutso 20:12), momwe machimo a mtundu wa anthu analembedwa. Chifukwa chimene wansembe anali kuika mwazi wa nsembe yauchimo pa nyanga za pa guwa la nsembe yopsereza chinali chakuti afufute maina ndi zolakwa zawo zinalembedwa mu Buku Lachiweruzo. Mwazi ndi moyo wa thupi lonse. Nsembe inali kuchotsa machimo a Israyeli ndipo mbuzi yamoyo inali kuphedwa kuti alipire mphoto ya uchimo. Mulungu anawalola kupha nyama ya nsembe kuti alole chiweruzo cha machimo awo. Ichi chinali chizindikiro cha nzeru Yake ndi chikondi kwa ife.
Yesu anabwera padzikoli ngati nsembe ya uchimo kotero kuti akwaniritse chikonzero cha Mulungu. Yesu anachotsa machimo adziko kudzera mu nsembe Yake. Ngati tingaone pa mawu a lonjezo limeneli, tikuona, “Koma kunakomera Yehova kumtundudza; anammvetsa zowawa” (Yesaya 53:10) kapena “Amene acotsa cimo lace la dziko lapansi” (Yohane 1:29).
“Pakuti kwa ife Mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wa mwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lace, ndipo adzamucha dzina lace Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere. Za kuenjenjezera ulamuliro wace, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wacifumu wa Davide, ndi pa ufumu wace, kuukhazikitsa, ndi kuucirikiza ndi ciweruziro ndi cilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Cangu ca Yehova wa makamu cidzacita zimenezi.” (Yesaya 9:6-7).
Lonjezo lodabwitsa ndiponso labwino linali lakuti Yesu adzakwaniritsa chifuniro cha Mulungu ndi kupatsa okhulupilira onse mtendere pochotsa machimo adziko. Lonjezo la Mulungu linali lonjezo la chikondi, limene anakonza kuti abweretse mtendere ku mtundu wa anthu onse. Ichi ndi chimene Mulungu anatilonjeza, ndipo ichi ndi chimene Iye anachita.
Mateyu 1:18 ikuti, “Ndipo kubadwa kwace kwa Yesu Kristu kunali kotere: Amai wace Mariya anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera.” “Yesu” kutanthauza Mpulumutsi, amene adzapulumutsa anthu Ake ku machimo awo. “Kristu” kutanthauza Mfumu Yodzodzedwa, Mfumu Yesu analibe machimo, ndipo ndi Mfumu yathu ndiponso Mpulumutsi amene anabadwa kwa namwali ndi cholinga choti apulumutse anthu Ake ku machimo awo.
“Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo adzamucha dzina lace Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ace ku macimo ao. Ndipo zonsezi zinakhala kuti zikacitidwe conenedwa ndi Ambuye mwa mneneri” (Mateyu 1:21-22).
Yesu ananyamula machimo onse adziko limodzi ndi Iye kudzera mu ubatizo Wake
Munalembedwa mu Mateyu 3:13-16, “Pamenepo Yesu anacokera ku Galileya nadza ku Yordano kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye. Koma Yohane anati amkanize, nanena, Ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi? Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero. Pamenepo anamlola Iye. Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anaturuka m’madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye”
Yohane Mbatizi waonekera mu ndimeyi. Kodi n’chifukwa chiani Yesu anafunikira kubatizidwa ndi Yohane? Yesu anafunikira kubatizidwa kuti anyamule machimo onse adziko, ndi kuwachotsa onse mogwirizana ndi chikonzero cha Mulungu.
“Ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lace” (Yesaya 9:6). Apa “boma” likutanthauza kuti Yesu Ndi Iye amene ali ndi ulamuliro ndiponso mphamvu ngati Mbuye wa Kumwamba, ngati Mfumu yadziko. Uwu ndi ulamuliro omwe unapatsidwa kwa Yesu Kristu yekha. Yesu anachita chinthu chodabwitsa kuchotsa machimo onse a mtundu wa anthu. Chinthu chabwino chimenechi chinali chakuti Iye abatizidwe ndi Yohane. Chimene Yesu anatanthauza pamene ananena kuti “Pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero” ndi chakuti kuchotsa machimo onse adziko kunali kwabwino ndiponso koyenera.
Aroma 1:17 akuti, “Pakuti m’menemo caonetsedwa cilungamo ca Mulungu cakucokera kucikhulupiriro kuloza kucikhulupiriro.” Chilungamo cha Mulungu chikuvumbulidwa mu uthenga wabwino. Kodi uthenga oona wa madzi ndi Mzimu umavumbulutsadi chilungamo cha Mulungu? Inde! Uthenga wabwino oona ndi wakuti Yesu Kristu anachotsa machimo onse adziko kudzera mu ubatizo ndiponso kupachikidwa Kwake. Uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndi uthenga wabwino okoma momwe chilungamo cha Mulungu chavumbulutsidwa. Kodi Yesu anachotsa bwanji machimo adziko? Iye anachotsa machimo onse adziko pamene Yohane anamubatiza Iye mu Mtsinje wa Yordano.
“Chilungamo chonse” ndi “πᾶσαν δικαιοσύνην (pasan dikaiosune)” mu Chigiriki. Ichi chikutanthauza kuti Yesu anachotsa machimo onse a mtundu wa anthu m’njira yachilungamo ndiponso yodabwitsa kwambiri. Zikutanthauza kuti kuyeretsa kwa machimo adziko kumene Yesu anachita kunali kwachilungamo ndiponso koyenera. Yesu anayenera kubatizidwa ndi Yohane kuti achotse machimo adziko.
Mulungu anadziwa kuti ubatizo wa Yesu unali ofunikira kwambiri kuti abweretse mtendere ku mtundu wa anthu. Yesu sakanakhala Mpulumutsi wathu, ngati sakanabatizidwa ndi Yohane ndi kukhetsa mwazi pa Mtanda. Yesu anagwira ntchito ngati nsembe yauchimo pamene anali kuchotsa machimo onse adziko.
Yesu anati mu Yesaya 53:6, “Tonse tasocera ngati nkhosa; tonse tayenda yense m’njira ya mwini yekha; ndipo Yehova anaika pa Iye mphulupulu ya ife tonse.” Yesu anayenera kulola machimo onse adziko kuti achite chifuniro cha Mulungu. Ichi ndi chifukwa chake Yesu anabwera ngati nsembe yauchimo mu thupi la umunthu ndipo anabatizidwa ndi Yohane.
Yesu anayenera kulola machimo onse a mtundu wa anthu ndi kuweruzidwa chifukwa cha iwo kotero kuti akwaniritse chikonzero cha Mulungu ndi kuonetsa chikondi Chake chosafa. Pamene Yesu anaturuka m’madzi atabatizidwa, Mulungu anati, “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera” (Mateyu 3:17).
Mwana wakhanda anabadwa kwa ife
“Pakuti kwa ife Mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wa mwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lace, ndipo adzamucha dzina lace Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere” (Yesaya 9:6). Yesu ndi Mwana wa Mulungu. Yesu ndi Mulungu wa Zolengedwa amene analenga dziko lonse. Iye si Mwana yekha wa Mulungu Wamphamvu yonse, Iyenso ndi Mlengi ndiponso Mfumu ya Mtendere. Yesu ndi Mulungu amene anapereka chimwemwe ku mtundu wa anthu.
Yesu ndi Mulungu wachoonadi. Iye anachotsa machimo athu onse, anatipulumutsa, ndi kutipatsa mtendere. Kodi muli uchimo m’dziko lino? Ai, mulibe uchimo. Chifukwa chomwe tingakambire kuti mulibe uchimo ndi chakuti timakhulupilira mu uthenga wabwino okoma, umene umanena kuti Yesu anatsuka machimo onse adziko kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi Wake wa pa Mtanda. Yesu sananene bodza kwa ife. Yesu analipira mphoto ya uchimo ndi ubatizo Wake komanso mwazi. Iye analola aliyense amene amakhulupilira m’menemu kukhala mwana Wake ndi kupereka mtendere kwa ife tonse. Iye anatipanga kuti tikhale ngati ana Ake oyeretsedwa m’chikhulupiliro kwamuyaya. Ndikuyamika Ambuye ndi kupereka mathokozo kwa Iye.
Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!
Yohane 1:29 akuti, “M’mawa mwace anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” Yesu Kristu anaonekeranso kutsogolo kwa Yohane Mbatizi tsiku lotsatira atachotsa machimo onse adziko kudzera mu ubatizo. Yohane Mbatizi anachitira umboni kwa Yesu ponena kuti, “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” Anachitiranso umboni mu Yohane 1:35-36, “M’mawa mwacenso analikuimirira Yohane ndi awiri a akuphunzira ace; ndipo poyang’ana Yesu alikuyenda, anati, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu!”
Yesu anali Mesiya amene anabwera ngati Mwana Mwanawankhosa wa Mulungu, monga m’mene Mulungu analonjezera mu Chipangano Chakale. Mesiya Yesu Kristu anabwera kwa ife ngati Wodabwitsa, Wauphungu ndiponso Mulungu wamphamvu, ndipo anabatizidwa kuti atipulumutse ife ku machimo athu onse. Mwana wakhanda anabadwa kwa ife. Iye anavomera machimo onse adziko kudzera mu ubatizo Wake ndi Yohane, analipira mphoto ya uchimo, ndi kukhala Mwana wamfumu wa mtendere amene amatipatsa ife mtendere ndi chikhululukiro cha machimo athu onse. “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!”
Anthu poyamba analibe chisankho china koma kufa chifukwa cha machimo awo. Anthu anayenera kuchita machimo osawerengeka chifukwa cha kubadwa kwawo kwauchimo ndipo pomaliza aweruzidwire ku Gahena. Ankakhala ndi miyoyo yozunzika; panalibe wina wa iwo amene akanatha kulowa kapena kulota za Ufumu wa Mulungu chifukwa cha kufoka kwawo. Yesu Kristu, amene ndi Mulungu wathu, kulola machimo awo onse pamene anabatizidwa ndi Yohane mu Mtsinje wa Yordano ndipo anaweruzidwa chifukwa cha zolakwa zawo. Pa nthawi ya imfa Yake, Kristu anati, “Kwatha” (Yohane 19:30). Uku kunali kulira kwa umboni Wake ku choona chakuti Yesu anapulumutsa mtundu onse wa anthu ku machimo awo ndi imfa, ndipo kuti motero anapulumutsa aliyense kwathuthu amene anakhulupilira mu uthenga wabwino okoma.
“Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene acotsa cimo lace la dziko lapansi!” Kodi mudziwa kumene machimo onse adziko ali? Kodi sali pa thupi la Yesu Kristu? Kodi machimo onse ndi zolakwa zimene zimatichepetsa mdzikoli zilikuti? Zonse zinaperekedwa kwa Yesu Kristu. Kodi machimo athu onse ali kuti? Ali mu thupi la Iye amene ali ndi ulamauliro pa mapewa ake; iwo ali mthupi la Mulungu Wamphamvu zonse.
Machimo onse kuchokera panthawi yobadwa kufikira ku manda!
Timachita uchimo pa miyoyo yathu yonse. Timachita machimo kuyambira tsiku la kubadwa kufikira tsiku limene tinakhala ndi zaka 20. Kodi machimo onse amene tinachita kwa zaka 20 anapita kuti? Anaperekedwa pa thupi la Yesu Kristu. Machimo amene tinachita pakati pa zaka 21 ndi 40 anaperekedwanso pa Yesu. Zilibe kanthu kuti munthu wakhala zaka zambiri, machimo amene anachita kuyambira pachiyambi cha moyo wake kufikira kuchimaliziro anaperekedwa kwa Yesu Kristu. Machimo onse amene mtundu wa anthu unachita, kuyambira pa Adamu kufikira kwa munthu omaliza padziko lapansi, anaperekedwa kwa Yesu. Ngakhale machimo a ana athu ndi zidzukulu anaperekedwa kale kwa Yesu. Machimo onse anaperekedwa kwa Yesu pa nthawi imene anabatizidwa.
Kodi mudakali machimo m’dziko lino? Ai. Osati ngakhale amodzi otsala. Palibe tchimo lotsala m’dziko lapansi chifukwa timakhulupilira mu uthenga wabwino okoma umene Yesu Kristu anapereka kwa ife. Kodi muli ndi uchimo mu mtima mwanu? Ai. Ame! Timakhulupilira mu uthenga wabwino okoma umene Yesu Kristu ananena kuti unatipulumutsa ku machimo athu. Tikutamanda Yesu wamphamvu yonse pakuchita nchito yabwino imeneyi kwa ife.
Yesu anabwezeretsa miyoyo yathu inasowa kwa ife. Tsopano timakhulupilira mu uthenga wabwino okoma kotero kuti tithe kukhala limodzi ndi Mulungu. Ngakhale anthu amene anali adani a Mulunguochimwa amene analibe chisankho chilichonse koma kubisala mu thengo la mdimatsopano angapulumutsidwe ku machimo awo pokhulupilira mu uthenga wabwino okoma.
Uthenga wabwino okoma ukutiphunzitsa kuti Ambuye anatsuka machimo athu onse pamene Iye anabatizidwa ndi Yohane, kupachikidwa ndi kuukitsidwa. Tinakhala ana oyeretsedwa a Mulungu mwa kukhulupilira mu uthenga wabwino wa Yesu. Yesu anapereka thupi Lake ngati nsembe ku machimo athu. Iye, Mwana wa Mulungu Wamphamvu zonse, amene sanachitepo tchimo lililonse mdziko lino, anachotsa machimo onse adziko ndi kupulumutsa aliyense amene amakhulupilira mwa Iye. Yesaya 53:5 akuti, “Koma Iye analasidwa cifukwa ca zolakwa zathu, natunduzidwa cifukwa ca mphulupulu zathu.”
Yesu anachotsa machimo onse adziko, kuphatikizapo tchimo loyamba ndiponso uchimo wamasiku onse ndi kusasiya cholakwa ngakhale chimodzi. Iye analipira mphoto ya uchimo ndi imfa Yake ya pa Mtanda ndipo motero anatipulumutsa ku machimo athu onse. Yesu anatsuka machimo onse adziko kudzera mu uthenga wabwino okoma umenewu. Tapeza moyo watsopano kudzera mwa Yesu. Iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma umenewu salinso akufa muuzimu. Tsopano tili ndi tsopano ndiponso moyo wamuyaya, pakuti Yesu analipira mphoto zonse za uchimo. Takhala ana a Mulungu pokhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa Yesu Kristu.
Kodi mumakhulupilira kuti Yesu Kristu ndi Mwana wa Mulungu? Kodi mumakukhulupiliranso kuti ndi Iye Mpulumutsi wanu? Ine ndimatero. Yesu Kristu ndi Moyo kwa ife. Tinapeza moyo watsopano kudzera mwa Iye. Tinayenera kufa chifukwa cha machimo athu ndi zolakwa zathu. Koma Yesu analipira mphoto ya uchimo kudzera mu ubatizo Wake ndi imfa ya pa Mtanda. Iye natiombola ku ukapolo wathu wakuchimwa, ku mphamvu ya imfa, ndiponso ku dzingwe za Satana
Ambuye ndi Mulungu amene anatipulumutsa ku machimo athu ndi kukhala Mpulumutsi wa aliyense amene amakhulupilira mwa Yesu. Pamene tiona mu Ahebri 10:10-12, 14 ndiponso 18, tingaone kuti Ambuye anatiyeretsa ife kuti pasakhalenso kufunika kwa kulandiranso chikhululukiro cha machimo. Timalowa mu Ufumu wa Kumwamba pokhulupilira mwa Yesu. Tinayenera kufa chifukwa cha machimo athu ndi zolakwa, koma tsopano titha kulowa Kumwamba ndi kusangalala ndi moyo osatha mwa kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi.
“Mbusa wabwino ataya moyo wace cifukwa ca nkhosa” (Yohane 10:11). Ambuye wathu anabwera m’dzikoli ndi cholinga chakuti atipulumutse ife ku machimo adziko kudzera mu ubatizo Wake, imfa Yake ya pa Mtanda, ndiponso kuuka Kwake. Iye amaperekenso kukhazikika kwa Mzimu Woyera kwa iwo amene analandira chikhululukiro cha machimo awo pokhulupilira mu choonadi chimenechi, Zikomo, Ambuye. Uthenga wabwino wanu ndi uthenga wabwino okoma, umene ungapatse okhulupilira kukhazikika kwa Mzimu Woyera, Aleluya! Ndikuyamika Ambuye.