(Yohane 7:37-38)“Koma tsiku lomariza, lalikurulo la phwando, Yesu anaimirira napfuula, ndi kunena, Ngati pali munthu akumva ludzu, adze kwa Ine, namwe. Iye wokhulupirira Ine, monga cilembo cinati, Mitsinje ya madzi a moyo idzayenda, kuturuka m’kati mwace.”
Kodi ndi ndani angamwe madzi amoyo a Mzimu Woyera?
Iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda.
Madzi amoyo a Mzimu Woyera amayenda m’mitima ya iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma. Yohane 7:38 inena kuti, “Iye wokhulupirira Ine, monga cilembo cinati, Mitsinje ya madzi a moyo idzayenda, kuturuka m’kati mwace.” Ichi chikutanthauza kuti muli chipulumutso choona ndi chikhululukiro cha machimo kwa iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma umene Mulungu anatipatsa ife.
Kodi kukhazikika kwa Mzimu Woyera kumachitika liti? kukhazikika kwa Mzimu Woyera kungapezeke pamene munthu wamvera ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino oona, umene ukunena kuti Yesu Kristu anachotsa machimo onse a dziko kudzera mu ubatizo Wake ndi Yohane. Munthu ndiyeno angamwe madzi amoyo a Mzimu Woyera. Iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera, ndipo angalawe kumveka kwa madzi Auzimu amoyo atsopano kusefukira ndi kunyowetsa mitima yawo youma nthawi zonse pamene akulalikira kapena kumvera mawu a Mulungu.
Madzi amoyo a Mzimu Woyera amayenda m’mitima ya iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, umene umanena kuti Ambuye anabwera kudzikoli kuti apulumutse ochimwa onse ku machimo awo. Mzimu Woyera ndi choonadi chimene sichingapatulidwe ku uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, ndi kupumula mu anthu amene amakhulupilira mawu a Mulungu.
Aliyense amene akufuna kumwa madzi amoyo a Mzimu Woyera ayenera kulandira chikhululukiro cha machimo ake mwa kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda. Madzi amoyo amenewa a Mzimu Woyera amapezeka m’mitima mwa iwo amene amakhulupilira m’mawu a Mulungu. Anthu amene amakhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ali ndi madzi amoyo a Mzimu Woyera, amene amayenda ngati mtsinje, kukhamukira m’mitima yawo. Ngakhale panthawi ino, madzi amoyo a Mzimu Woyera akutuluka ngati madzi m’mitima ya iwo amene analandira chikhululukiro cha machimo awo pokhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa ubatizo Yesu Kristu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda.
Komabe, palibe ngakhale mdontho limodzi la madzi amoyo a Mzimu Woyera oyenda m’mitima ya iwo amene sakukhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa choonadi. Kufikira nditakhulupilira ndi kudziwa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, ndinalibe mdontho ngakhale limodzi la madzi amoyo Auzimu oturuka mu mtima mwanga. Pa nthawi imeneyo, ngakhale kuti ndinali kukhulupilira kwambiri mwa Yesu Kristu, sindinkadziwa ubwino wake wa madzi amoyo a Mzimu Woyera chifukwa ndinalibe Mzimu Woyera mu mtima mwanga. Komabe, tsopano ndili ndi uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu, ndiponso madzi amoyo a Mzimu Woyera omwe amatuluka momasuka kuchoka mu mtima mwanga.
Tsopano madzi amoyo a Mzimu Woyera amatuluka mu mtima mwanga, ndiponso mwa mitima ya iwo amene amamvera ndi kukhulupilira mu mawu a Mulungu. Monga m’mene Yesu ananena kuti, “Ngati pali munthu akumva ludzu, adze kwa Ine, namwe,” madzi a moyo a Mzimu Woyera amatsitsimutsa ena kudzera mwa Akristu obadwa mwatsopano amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. Madzi amoyo amenewa amatuluka mu mtima mwanga pamodzi ndi chikhulupiliro mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ngakhale pa nthawi ino, kulola ena kuti amwe m’menemo. Mulungu amalola kuti madzi amoyo a Mzimu Woyera atuluke mu mtima mwanga ngati Mtsinje. Ichi ndi chodziwika ndi iwo okha amene ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera.
Monga kunalembedwa mu Chivumbulutso kuti palibe amene amadziwa kuchotsako iwo amene anaulandira, kukhazikika kwa Mzimu Woyera ndiponso madzi amoyo ndi chinsinsi chodziwika kokha kwa iwo amene akudziwa ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. Motero, Muyenera kudziwa kuti ndi mwa ndani m’mene Mzimu Woyera umakhala. Muyenera kudziwa kuti kukhazikika kwa Mzimu Woyera kumaperekedwa kwa okhawo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino wa Yesu.
Ndinkakhulupilira mu mwazi okha wa pa Mtanda
Ngakhale kuti ndinali kukhulupilira mu mwazi okha wa Yesu a pa Mtanda kwa zaka zopitilira khumi, uchimo unali udakali mu mtima mwanga. Pa nthawi imeneyo, ndinali ndi chikhulupiliro chakuti machimo anga anali kukhululukidwa mwa kudzera m’mwazi okha wa Yesu. Komabe, sindinalandire ngakhale chikhululukiro cha uchimo kapena kukhazikika kwa Mzimu Woyera kudzera mu mtundu wa chikhulupiliro umenewu, ndipo kunali chabe chisokonezo ndiponso kupanda kanthu m’moyo wanga. Chizindikiro chokhako chimene chinaonetsa chikhulupiliro changa mwa Yesu ndi choona chakuti ndinali kupezeka ku mpingo.
Apo ndi pamene ndinayamba kuganizira za chikhulupiliro changa. ‘Kodi ndinalandiradi Mzimu Woyera?’ Pamene ndinayamba kukhulupilira mwa Yesu, mtima wanga unali ofunitsitsa chikondi Chake ndipo ngakhale ine ndinali ndi mphatso ya m’malilime. Koma kodi chinadza mwa ine ndi chiani? Ndinazindikira kuti chotentha chotengeka chimene ndinkamva sichinali chizindikilo cha kukhazikika kwa Mzimu Woyera ndiponso kuti sindinalandire Mzimu Woyera konse. Ndinakhulupilira mwa Yesu, koma Mzimu Woyera ndiponso madzi amoyo a Mzimu Woyera sanali mu mtima mwanga.
Sichinali chofunikira ngati mtima wanga sunali otentha kapena ozizira, popeza chikhulupiliro changa chinali kuchokera mu [4]Chicalvin. Mafunso amene ndinafunikira kuyankha anali otsatirawa:
(1) Kodi Mzimu Woyera umakhala mwa ine? ─ Ai. Sindikutsimikiza kuti Iye ali mwa ine. ─
(2) Kodi muli uchimo mwa ine? ─ Inde, ulimo. ─ Munalidi uchimo mwa ine panthawiyo, ngakhale kuti ndinkakhulupilira mu mwazi wa Yesu a pa Mtanda. Ndinali ndi uchimobe mu mtima mwanga, ngakhale kuti ndinkakhulupilira mwa Yesu ndi kumanena mapemphero a kulapa masiku onse. Uchimo mu mtima mwanga sunatsukidwe onse mulimonse m’mene ndingayesere molimbika.
4Ndondomeko ya kumasulira kwa Chikristu analemba Yohane Kavini. Chimatsindika pa kukonzedweratu komanso chipulumutso. Mfundo zisanu za Chicalvini zinatuluka kuchokera ku yankho la Chiarminia. Chicalvini chimaphunzitsa kuti: 1) Kuonongeka kwathuthu: kuti munthu amagwidwa ndi uchimo m’mbali zonse za kukhala kwake : thupi, moyo, maganizo, ndiponso chikumbumtima, 2) Chisomo chosayenera: kuti chisomo cha Mulungu kwa munthu ndi chisankho Chake kotheratu ndipo zilibe kanthu ndi zochita za munthu. Ndi chosayenera kwanthunthu kwa munthu, 3) Chitetezero chochepa: Kuti Kristu sananyamule machimo a munthu aliyense amene anakhalako koma m’malo mwake anasenza machimo a okhawo amene anasankhidwa mu chipulumutso, 4) Chisomo chosaletseka: kuti muitano wa Mulungu kwa munthu ku chipulumutso sungaletseke, 5) Chipiliro cha Woyera mtima: Kuti ndikosatheka kutaya chipulumutso cha munthu. Koma mungasiyanitse poyera ziphunzitso zake ku uthenga wa madzi ndi Mzimu, makamaka mu ziphunzitso zake za chitetezero chochepa. |
‘Kodi ndingalandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera? ‘Kodi ndingatsuke motani uchimo mu mtima mwanga?’ Awa anali mavuto awiri amene ankandivutitsa omwe ndinali nawo mu m’maganizo mwanga, ngakhale pamene ndinayamba kukhulupilira mwa Yesu. Ndinali kunenera m’malilime pamene ndinayamba kukhulupilira mwa Yesu ndiponso ndinakhulupiliranso kuti machimo anga anayeretsedwa ndikuyamikira chikhulupiliro changa m’mwazi wa Yesu.
Komabe, pamene nthawi inali kupita, machimo ochuruka anadzala mu mtima mwanga. Ndinali odzala ndi uchimo. Mapempehero a kulapa kapena kusala kudya sankatsuka machimo mu mtima mwanga popeza ndinkakhulupilirabe mu mwazi okha wa Yesu. Ndinadankhawa kwa nthawi yaitali chifukwa cha machimo anga amasiku onse. Pamene ndinali kudandaula kwambiri, ndipamene ndinali kulalikira uthenga wabwino wa Yesu kwa ena mwamphamvu. Ndinalinso kupezeka ku mpingo ngakhale pafupipafupi ndi kuzipereka ndekha pa kutumikira Yesu, ndikudalira pa mwazi Wake.
Komabe, pamene nthawi inali kupita, machimo amasiku onse mu mtima mwanga anali kunditsekereza kukhala ndi chikhulupiliro choona. Kunali kovuta kukhulupilira mwa Yesu kuposa kale. Ndinayesa kudalira kwambiri mu mwazi wa Yesu ndi kuika patsogolo mphamvu zanga ndi kuonjezera kuzipereka kwanga kwa Mulungu. Komabe, kupanda kanthu kwa mtima wanga kunakula. Chikhulupiliro chotere chinasiya ine ndikuzimva opanda kanthu ndiponso waulesi, ndikunditembenuza kukhala Mkristu wachinyengo amene ndinkasamalira maonekedwa akunja kokha. Kuganiza pa ine ndekha, ‘Kukhulupilira mwa Yesu kuli ngati kotere kwa aliyense, si kwa ine ndekha!’ Ndinayesa kukana kuti chikhulupiliro changa chinali chosocheretsedwa. Komabe, mwazi wa Yesu ndi mapemphero a kulapa sanatsukebe machimo anga amasiku onse.
Nanga kodi ndi mwa chikhulupiliro chotani chimene machimo anga amasiku onse angayeretsedwe? Machimo anga amasiku onse akanatsukidwa pokhapo kudzera mu chikhulupiliro changa kuti machimo anga onse anaperekedwa kwa Yesu pamene anabatizidwa mu Mtsinje wa Yordano. Ichi ndi chimene chinalembedwa mu Mateyu 3:13-17. Ndiyeno kodi ndi chifukwa chiani machimo anga amasiku onse sanatsukidwe ndi mwazi wa Yesu? Sindinadziwe ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma, umene uli ndi tanthauzo la ubatizo wa Yohane pa Yesu.
Kodi ichi chikutanthauza kuti machimo onse adziko lapansi anatsukidwa kudzera mu ubatizo wa Yesu? Inde, icho ndi choona. Baibulo limachitila umboni pa chimenechi ponena kuti, “Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu” (Yohane 3:3-5). Yesu anabwera mdzikoli ndi kulandira machimo onse a dziko kudzera mu ubatizo Wake ndi Yohane.
Ndinali okaikirabe za chimenechi ndi funaniza Chipangano Chakale ndi Chipangano Chatsopano kuti ndilongosole chimenechi. zotsatira zake ndinapeza kuti zinali zoona. Machimo onse a dziko anaperekedwa pa Yesu pamene anabatizidwa, ndipo machimo anga onse anaperekedwanso pa Iye panthawi imeneyo. Ndinayeretsedwa kudzera m’chikhulupiliro changa m’mawu amenewa. Ndinazindikira kuti awa ndi mawu a choonadi monga analembedwera mu Baibulo ndipo ndi uthenga wabwino okoma kwambiri m’dziko lapansi.
Kuonjezerapo, ndinazindikira kuti ndi chifukwa chake machimo anga sanafafanizidwe kudzera mu chikhulupiliro changa cha mu mwazi wa Yesu okha. Chifukwa chinali chakuti sindinapereke machimo anga amasiku onse kwa Yesu pamene sindinali kudziwa choonadi cha ubatizo Wake mu Mtsinje wa Yordano. Pomaliza ndinakumana ndi choonadi. Ndinaphunzira kuti Yesu anadza m’dziko lino chifukwa cha ine, ndipo kuti anachotsa machimo onse a dziko kudzera mu ubatizo Wake, ndipo pamapeto pake anapachikidwa kuti atiombole ife ku machimo onse a dziko. Ndinaphunziranso ndi kukhulupilira mu choonadi kuti cholinga cha ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda chinali kuchotsa machimo onse adziko. Tsopano ndine olungama ndikuyamikira chikhulupiliro changa mu uthenga wabwino okoma umene Yesu anapereka kwa ife, ndiponso chifukwa chakuti machimo anga onse akhululukidwa.
Sichinali chiphunzitso cha mpingo chimene chinafafaniza machimo anga, unali ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda umene anachita choncho. Choonadi chimenechi chinali mu uthenga wabwino okoma. Ndinapulumutsidwa ku machimo anga onse ndi kukhala olungama osati kudzera mu chikhulupiliro changa cha mwazi wa Yesu okha, koma kudzera mu chikhulupiliro changa kuti ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda ndi za chipulumutso changa.
Chinthu chimodzi chimene ndikufuna kuyamika ndi chakuti Mzimu Woyera wa Mulungu unadza pa ine pamene ndinayamba kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma. Tsopano Mzimu Woyera umakhala mwa ine pamodzi ndi mawu a ubatizo wa Yesu ndi Yohane komanso mwazi Wake wa pa Mtanda.
Ndikuyamikira Ambuye amene anandipatsa uthenga wabwino okomawu ndiponso amene anandilola kulalikira zikhulupiliro zofanana ndi zija za Atumwi a Yesu. Mulungu anandipatsa mphatso ya Mzimu Woyera, ngakhale kuti chinthu chimodzi chimene ndinachita chinali kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma. Tsopano ndingapereke uthenga wabwino umenewu ndi kulemekeza kwakukulu ndiponso chitsimikizo kwa anthu onse a pa dziko lapansi. Motsimikiza ndingawauze kuti kukhulupilira m’mwazi okha wa Yesu sikuzachotsa machimo awo onse!
Koma ndingawauze kuti machimo awo onse adzatsukidwadi pokhapo ngati akhulupilira mu uthenga wabwino okoma, umene umanena za ubatizo wa Yesu ndi Yohane ndiponso mwazi Wake wa pa Mtanda. Ndiribe ngakhale ndi manyazi nkomwe pamaso pa Mulungu pamene ndikulalikira uthenga wabwino okomawu. Tsopano ndingathe kulalikira molemekeza uthenga wabwino okoma umenewu wa kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu kwa anthu onse a pa dziko lapansi. Ndikupereka kuthokoza kwa Ambuye. Ndikuthokoza Ambuye amene analola kuti ndimwe madzi amoyo a Mzimu Woyera pondipatsa ine uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Muyezo wa Kuchipatala waonetsa kuti uthenga wabwino oona ndi wa madzi ndi Mzimu
Kodi munalandiradi chikhululukiro cha machimo anu ndiponso kukhazikika kwa Mzimu Woyera? Kodi munganene motani ngati uthenga wabwino ndi oonadi? Nthawi ina ndinachita muyezo pa anthu amene anali kufuna kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma umene unapatsidwa kwa ife ndi Yesu. Kwa munthu m’modzi ndinalalikira uthenga wabwino wa mwazi wa Yesu wa pa Mtanda. Ndinamuuzanso iye kuti muyenera kukhala mulibe uchimo mwa Yesu. Kwa munthu winanso ndinalalikira uthenga wabwino okoma wa ubatizo wa Yesu ndi Yohane ndi mwazi Wake wa pa Mtanda. Chotsatira chake ndi chinali chakuti munthu amene analandira chikhululukiro cha machimo ake mwa kukhulupilira kokha m’mwazi wa Yesu ananena kuti anayenera kupitilizabe kukhululukidwa ku machimo ake amasiku onse. Koma munthu amene ankakhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi, kumbali inayi, ananena kuti tsopano wakhala munthu wangwiro opanda uchimo.
Iye ananena kuti alibe uchimo mu mtima mwake chifukwa anakhalupilira mu choonadi chakuti Yesu ananyamula machimo ake onse ndipo anaweruzidwa chifukwa cha iwo. Anatha kulandira Mzimu Woyera kwa Mulungu chifukwa anakhulupilira mu uthenga wabwino okoma, umene umanena kuti ubatizo wa Yesu ndi Yohane unatsuka machimo onse adziko lapansi.
Chifukwa chimene munthu uyu ananenera motero ndi chakuti analibenso uchimo mu mtima mwake chinali chifukwa analandira Mzimu Woyera mu mtima mwake kudzera mu chikhulupiliro chake mu uthenga wabwino okoma. Mzimu Woyera unamupatsa iye chitsimikizo yonena kuti alibe uchimo mu mtima mwake. Mulungu amapereka kukhazikika kwa Mzimu Woyera kwa iwo amene amakhulupilira ubatizo wa Yesu ndi Yohane ndiponso mwazi Wake wa pa Mtanda. Kodi ndi mwa ndani m’mene Mzimu Woyera umakhala? Mzimu Woyera umapatsidwa ngati mphatso kwa iwo amene akhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa ubatizo wa Yesu ndi Yohane ndiponso mwazi Wake wa pa Mtanda.
Kuona kokha chochitika kubwalo la Tsiku la Pentekosite lapangitsa anthu ambiri kuti asadziwe bwino choonadi cha kulandira Mzimu Woyera ndi kuika padera uthenga wabwino okoma. Anthu akuganiza kuti ngati angazipemphera ndi kufuna Mzimu Woyera kwambiri, azatha kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Kwa nthawi yaitali, Akristu kuzungulira dziko lonse lapansi sanalinso ndi ganizo ngakhale laling’ono la choonadi, limene linkanena kuti munthu angalandire Mzimu Woyera pongokhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi. Komabe, tsopano akapolo ambiri a Mulungu, amene analandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera kudzera mu chikhulupiliro chawo mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, analalikira uthenga ndi thandizo la Mzimu Woyera. Mwa ichi, anthu ambiri kuzungulira dziko lonse lapansi anaphunzira kulandira uthenga wabwino okoma umenewu ndi kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera.
Mulungu amalola anthu amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma umenewu kuti amvere kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Mu Baibulo, akunena kuti, “Ndipo kudzali m’masiku otsiriza, anena Mulungu, Ndidzathira ca Mzimu wanga pa thupi liri lonse” (Macitidwe a Atumwi 2:17). Komabe, munthu ayenera kudziwa kuti kuyesa kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera popanda kudziwa uthenga wabwino okoma ndi kulakwitsa. Palibenso njira ina yolandilira kukhazikika kwa Mzimu Woyera kuposa kulandira ubatizo wa Yesu ndi Yohane ndi mwazi Wake wa pa Mtanda.
Popeza Mulungu ananena kuti munthu angalowe mu Ufumu wa Kumwamba pokhapo ngati wabadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu, ndipo ndi obadwa mwatsopano okha amene ali ndi mphatso ya Mzimu Woyera, palibe chikaiko kuti aliyense amafuna kukhazikika kwa Mzimu Woyera kuti akalowe mu Ufumu wa Kumwamba. Kodi mungaganize bwanji za kulandira Mzimu Woyera kapena kulowa Kumwamba popanda kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu? Kulibe njira ya Kumwamba yoposa kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma. Mungalandire Mzimu Woyera pokhapo mwa kukhulupilira mu uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Monga m’mene timalipilira ndalama pamene tikugula chinthu, timalandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera pamene takhulupilira mu uthenga wabwino okoma.
Ndikufuna kukuuzani kuti ngati mukufunadi kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera, muyenera choyamba kudziwa ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Motero muzamva kulandira kwa Mzimu Woyera. Mungalandire kokha kukhazikika kwa Mzimu Woyera pokhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. Mulungu amafuna kuti akupatseni inu kukhazikika kwa Mzimu Woyera.
Ndimakhulupilira mu uthenga wabwino okoma ndipo pamene nthawi ikupita, ndimazimva kukhala wamphamvu kuti uthenga wabwino okoma umenewu omwe Mulungu anandipatsa ndi chinthu chokoma kwambiri ndiponso ndi chinthu chamtengo wapatali m’dziko lapansi. Ndikumva kuyamika kwa Mulungu. Kodi inunso mukumva chimodzimodzi? Tikuzindikira kuti iwo a ife amene talandira Mzimu Woyera tinadalitsidwa kwakukulu ndi Mulungu.
Ndikukupatsani uthenga wabwino wa m’mene mungalandilire kukhazikika kwa Mzimu Woyera mwa kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma. Anthu angaziyenereze okha kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera pokhapo ngati avomera uthenga wabwino odalitsika umenewu wa kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu.
Mu Yohane 7:38, Yesu anati, “Iye wokhulupirira Ine, monga cilembo cinati, Mitsinje ya madzi a moyo idzayenda, kuturuka m’kati mwace.” Ichi chikutanthauza kuti anthu amene analandira chikhululukiro cha machimo awo onse mwa kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma umene Yesu Kristu anawapatsa ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Madzi a moyo a Mzimu Woyera adzatuluka ngati mtsinje; mitima yawo. Anthu amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma umenewu adzaona kutuluka kwa madzi amoyo Auzimu.
Ngakhale kuti ndinali okhulupilira wakhama mwa Yesu ndisanabadwe mwatsopano kudzera mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, kunalibe madzi amoyo a Mzimu Woyera otuluka mu mtima mwanga. Komabe, nditakhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu, madzi amoyo anayamba kutuluka momasuka mu mtima mwanga monga kunalemedwa mu Baibulo. Ngakhale pa nthawi ino, madzi amoyo a Mzimu Woyera amayenda pamodzi ndi uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu umene Mulungu anapereka kwa ine. Madzi amoyo a Mzimu Woyera amatuluka ambiri mu mtima mwanga kuzungulira chaka chonse. Ndinayamba kugwira ntchito ya mlaliki, kulalikira uthenga wabwino okoma, nditalandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera.
Chibvomerezo changa cha chikhulupiliro pamene ndinakhulupilira mu uthenga wabwino okoma ndi kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera
Inali nyengo yakutha kwa chilimwe m’chaka changa cha m’makumi awiri. Chilimwecho makamaka chinapangitsa kuti ine ndiganizire za kusapewa imfa kwanga. Moyo wanga chaka chimenecho unalembedwa ndi chisokonezo, kupanda kanthu ndiponso mdima chifukwa cha machimo mu mtima mwanga. Ndinali kupita ku njira yolakwika, kopanda kudziwa kuti njira iti imene ndiyenera kupita. Thupi langa linali kuyamba kudwala ndipo kupanda kanthu mu mtima mwanga kunakula.
Chifukwa cha machimo anga, ndinali osokonezeka kwambiri ndipo sindinali kudziwa chimene chinali kuyambitsa. Ndinalibe chisankho china koma kuyembekezera chiweruzo cha Mulungu pa kutha kwadzidzidzi kwa moyo wanga ndi kupempha chikhululukiro cha machimo anga. “Oho Ambuye, ndikufuna kulandira chikhululukiro cha machimo anga kudzera mu chikhulupiliro changa mwa inu ndisanafe. Ndiponso, chonde chizani nthenda ya mthupi langa!” Ndinapemphera ndi kupemphera.
Kochoka pamenepo, chiyembekezo chatsopano chinayamba kutuluka kuchokera pansi pa mtima wanga wankhawa. Mtima wanga unadzala ndi khumbo lofuna Mulungu, ndipo linali lotentha ngati mpira wamoto. Sunalinso othandiza: chinali chiyembekezo chatsopano chimene chinali kutentha ngati moto wamphamvumu mtima mwanga. Kuchokera pa nthawi imeneyo ndinayamba moyo watsopano wachipembezo, kukhulupilira kuti Yesu anafa pa Mtanda kuti apulumutse ine ku machimo anga.
Pasanathe nthawi yaitali zitapita zimenezo, ndinali odziwa kulankhula m’malilime. Pambuyo pake nthawi ndinapitiliza kukhetsa misozi pamene ndinkaganiza za mwazi wa Yesu omwe anakhetsa pa Mtanda. Ndinali othokoza kuti Iye anakhetsa mwazi Wake pa mtanda chifukwa cha ine.
Zitapita zimenezo ndinasiya moyo wanga wakale ndikupeza ntchito yatsopano imene inandilola kusunga Sabata lopatulika. Pa nthawi imeneyo, mtima wanga unali odzala ndi chikondi cha Yesu, ndi kusefukira ndi chiyamiko chosatha nthawi zonse ndikamva kuti Yesu anakhetsa mwazi pa Mtanda kuti apulumutse ine ku machimo anga. Mzimu wanga chipembedzo unayamba kukula, koma unali ochokera pa mawu a mwazi okha wa Yesu pa Mtanda.
Koma, pamene nthawi inali kupita, umoyo wanga wachipembezo unayamba kukhala ndi mlili ndi kuvutika chifukwa cha kufoka kwanga ndi machimo anga amasiku onse. Machimo anga onse sanatsukidwe kwathunthu chifukwa chikhulupiliro changa chinali mu mwazi wa Yesu okha pa Mtanda. Ndinayesa kutsuka machimo anga amasiku onse kudzera mu mapemphero a kulapa. Komabe, mapemphero amene ndinali kupereka ndi chiyembekezo chakuti ndizapeza chikhululukiro cha Mulungu sanatsuke kotheratu machimo anga. Ndi chifukwa chakuti sindinasunge malamulo a Mulungu. Machimo anga amasiku onse anayamba kuchuruka.
Ngakhale kuti machimo anga sankatsukidwa kotheratu kudzera mu mapemphero anga a kulapa, ndinalibe chisankho china koma kupitiliza kunena mapemphero amenewa. Ndinkakhulupilira kuti nthawi zonse ndikachimwa, ndingatsuke machimo anga kudzera mu mapemphero a kulapa ndiponso kuganizira za mwazi wa Yesu wa pa Mtanda. Pamene ndinali kupitiliza ndi moyo wanga wa chipembezo, ndi pamenenso machimo anga amasiku onse anali kuchuruka chifukwa cha kufoka kwanga. Kuvutika kwanga kunali kuonjezereka chifukwa cha machimo amenewa.
Ndinali kukhala Mkristu Wachifarisi, ndipo ndinasankhidwa kukhala dikoni ndipo mkupita kwa nthawi ndinakhala mlaliki mosasamala kanthu za kulemedwa kwa machimo anga. Ndinapita kukalalikira uthenga wabwino pamene ndamvera kuwawa kwa machimo anga amasiku onse, kuganiza kuti iyi inali njira yokhayo yakuyeretsa moyo wanga. Koma machimo anga amasiku onse sanali kutsukidwe kudzera mu mtundu uwu wa chikhulupiliro wochokera mu chiphunzitso ndiponso kudzipereka nsembe.
Ndinalinso ndi chomveka chakuti mwina ndingagwidwe ndi Satana. Ndinagwera mu kutsutsidwa chifukwa cha machimo anga amasiku onse ndipo ndinamva kukakamizika kuti ndingafe chifukwa cha zolakwa zanga. “Unachimwa, kodi sunatero?” Satana anapitiliza kutsutsa ndi kundizunza ine ndi uchimo.
Chikhulupiliro changa chinafika pafupi kugwa. Ndinazindikira kuti sindinkanatsuka machimo anga kudzera mu chikhulupiliro cha mu mwazi wa Yesu ndi mapemphero a kulapa okha, ndipo pothera pake ndinazipeza kuti ndili mu nyengo yokhumudwa.
Kuphunzira Chicalvini m’masukulu a zaumulungu, ndinakhala osangalatsidwa pa chifukwa chimene Yesu anabatizidwira ndi Yohane. Ndinafunsa M’phunzitsi wanga chifukwa chiani Yesu Kristu anabatizidwa ndi Yohane mu Yordano. Koma mayankho awo ankakhala ofanana, monga akuti anabatizidwa kuti aonetse kudzichepetsa Kwake kapena kulengeza kuti anali Mwana wa Mulungu. Koma, mayankho amenewa sanali okwanira kuti akhutilitsa chidwi changa.
Choonadi cha ubatizo wa Yesu ndi Yohane chinapangitsa ine kuti ndizindikire uthenga wabwino okoma
Pamene nthawi yanga ya ku seminale inatha, machimo anga sanatsukidwebe, ndipo ndinavutika pansi pa kulemera kwawo kwambiri kuposa pachiyambi. Kenako tsiku lina ndinamvetsetsa chifukwa chimene Yesu anabatizidwa ndiponso chifukwa chimene Iye ananenera kuti chilungamo chonse chidzakwaniritsidwa kudzera mu chochitika chimenechi. Unali uthenga wabwino okoma umene unanena kuti machimo anga onse anaperekedwa pa Yesu kudzera mu ubatizo Wake mu Mtsinje wa Yorodano. Mulungu anandithandiza kuzindikira choonadichi kudzera mu mawu Ake olembedwa.
Nditawerenga ndi kuwerenganso mawu a Mulungu, momwe uthenga wabwino okoma unalembedwa, pomaliza ndinazindikira choonadi kuti machimo anga onse anaperekedwa pa Yesu kudzera mu ubatizo Wake ndi Yohane ndiponso kuti anaweruzidwa chifukwa cha iwo pa Mtanda.
Apa ndi pamene ndinazindikira kuti kukhazikika kwa Mzimu Woyera kunabweradi mwa ine. Machimo anga onse mu mtima mwanga anakhululukidwa kotheratu pamene ndinamvetsetsa ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma. Machimo amene anandigwetsera ine mu kuvutika anatsukidwa kotheratu ndi mphamvu ya uthenga wabwino okoma. Machimo amenewo amene sanafufutike konse ngakhale ndinayesa kudzipereka ndekha kosalekeza ndi mapemphero a kulapa anasowa kwathunthu panthawi imodzi. Ndikupereka chiyamiko ndi mtima onse kwa Ambuye.
Ndimanena choonadi pamene ndikunena kuti machimo onse a dziko sangatsukidwe kudzera mu mwazi okha wa Yesu a pa Mtanda. Ubatizo wa Yesu ndi Yohane unatsogoleranso ku chikhululukiro cha uchimo. Tsopano aliyense ayenera kumvetsetsa ndi kukhulupilira kuti machimo onse anatsukidwa zikomo ku uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. Ndili ndi kukhazikika kwa Mzimu pansi pa mtima wanga chifukwa ndimakukhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu, komanso mawu a Mboni za Mulungu, amene ananena za Mwana Wake, anali okwanira kuchotsa machimo onse mu mtima mwanga. Ndinalandira Mzimu Woyera ngati nkhunda chifukwa cha chikhulupiliro changa mu uthenga wabwino okoma.
Kuyambira tsiku limenelo, Mzimu Woyera unkagwira ntchito mu mtima mwanga, unandilola ine kuti ndizigwira ntchito zauzimu, m’mawu ena, kuti ndilalikire uthenga wabwino okoma. Tsopano mulibe uchimo mu mtima mwanga. Ubatizo wa Yesu ndi Yohane ndiponso mwazi Wake wa pa Mtanda unachitira umboni ku chikhululukiro cha machimo anga ndipo ananditsogolera kuti ndikalandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Aleluya! Ndikutamanda Ambuye. Mzimu Woyera modekha unagwera pa ine ngati nkhunda ndipo unayamba kukhala mwa ine kuyambira tsiku limenelo limene ndinayamba kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Iye anayamba kugwira ntchito mu mtima mwanga nthawi zina ngati nkhunda, nthawi zina ngati kuphulika kwa ng’anjo.
Tsopano mungalandirenso kukhazikika kwa Mzimu Woyera ngati mungalole ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. Kodi simukufuna kulandira Mzimu Woyera ndi kutamanda Ambuye pokhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu pamodzi ndi ine? Kodi simukufuna kugwira ntchito pamodzi ndi ine ya kulalikira uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu ku dziko lonse lapansi? Uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu uzayeretsa inu ndi kukupatsani kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Chilungamo cha Mulungu chavumbulutsidwa mu uthenga wabwino kuchokera ku chikhulupiliro kupita kuchikhulupiliro. Ndi chifukwa chake kukhazikika kwa Mzimu Woyera kumapatsidwa kudzera m’chikhulupiliro chokha mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu.
Zinthu zodabwitsa zimene Mzimu Woyera wandichitira
Pamene ndinalandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera, ndinayamba kugwira ntchito ku mpingo wa tsopano pofuna kuti ndilalikire uthenga wabwino okoma. Mzimu Woyera unandipangitsa kuti ndilalikire mwamphamvu uthenga wabwino okoma.
Inali nthawi imeneyi pamene chochitika chotsatirachi chinachitika. Ku mzinda kumene ndinali kukhala, kunali osoka wina amene anali kuchita malonda ake ndi wogula malonda a ku dziko lina. Munthu ameneyu anali dikoni. Nthawi ina anaima pa malo ena ogona kuti achite malonda ndi wina ndipo anaona chizindikilo chathu pamenepo. Iye anakopeka ndi maitanidwe ndipo anayesa kuti akumane nane. Anakumana ndi ine ndi kunena kuti iye wakhala mu uchimo kwa nthawi yaitali. Kwa maola asanu a kukambirana pa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, pamapeto pake anazindikira choonadi cha chikhululukiro cha machimo. Iye anakhala obadwa mwatsopano, ndiponso analandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera pa nthawi imeneyo.
Pano pali nkhani ina imene inachitika pamene ndinapita kukaona nyumba ya mpingo. Ndinapeza nyumba yabwino ndiponso yaikulu. Koma pa nthawi imeneyo ndinali ndi ndalama zochepa zolipilira kuti ikhale nyumba ya mpingo wathu. Kunaoneka kosatheka kwa ine kuti ndithe kulipira nyumbayo chifukwa cha zochepa zimene ndinali kupeza. Komabe, Mzimu Woyera mwa ine unandiuza kuti “Khala wamphamvu ndiponso olimba.” Modabwitsa, ndinatha kupeza nyumba ya mpingo ndi kumachita ntchito Yake zikomo ku thandizo la Mzimu Woyera. Mzimu Woyera unandipangitsa kulalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu kuyambira nthawi imeneyo kupita mtsogolo. Mzimu Woyera okhala mu mtima mwanga uli ndi ine ngakhale pa nthawi ino, kuyambitsa kuti ndilalikire uthenga wabwino okoma ku anthu onse. Ndipo ndikuona onse amene akumva ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma umenewu akulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera.
Ndikuyamika Mzimu Woyera umene unandipatsa ine mphamvu yolalikira uthenga wabwino okoma umenewu. Ndikudziwa kuti ngakhale umoyo wanga onse uzakhala operewera kulemba zinthu zonse zimene Mzimu Woyera unachita kwa ine. Mzimu Woyera umandilola kukhala ndi madzi amoyo akutuluka momasuka mu mtima mwanga. Ndikupereka chiyamiko kwa Iye amene amakhala mwa ine.
Mzimu Woyera unadzala mpingo umene unayenda naye kudzera mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu
Nthawi ina ndinalowa m’chipululu kukalalikira uthenga wabwino okoma. Pa nthawiyo, Mulungu ananditsogolera ku mzinda waung’ono ndipo ndinakumana ndi kagulu kochepa ka anthu amene anali kufuna Mulungu. Mulungu ananditsogolera kuti ndilalikire uthenga wabwino okoma kwa iwo, umene unapangitsa iwo kuti iwo akhale ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Iwo analandilanso Mzimu Woyera mwa kumvetsera ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma. Mzimu Woyera unawatsogolera iwo kuti akhale antchito anga othandiza, ndipo ndinadza kuzalalikira uthenga wabwino okoma umenewu ku dziko lonse lapansi pamodzi nawo kuyambira pamenepo.
Pa nthawi imeneyo kanali kagulu kopchepa kokha ka anthu, osakhala kumbali ya chipembezo chilichonse. Anali kufuna kukhala mogwirizana ndi mawu a Mulungu, koma anali mofunitsitsa kulilira kwa Mulungu kuti awakhululukire machimo awo chifukwa cha ukapolo wa uchimo. Mzimu Woyera unanditsogolera ku gulu ili la anthu ndi kuyambitsa ine kulalikira uthenga wabwino okoma umenewu. Ndingaone kuti Mzimu Woyera unakonza iwo ndi ine kuti tikumane wina ndi mzake. Mulungu ananditsogolera ine kuti ndilalikire uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu kuyambira ndi ndondomeko yakaperekedwe ka nsembe monga kunalembedwa mu Levitiko, ndipo anthu analandira Mzimu Woyera kudzera mu mawu a uthenga wabwino okoma.
Mulungu anakhazikitsa mpingo wa Mzimu Woyera pamodzi ndi okhulupilira mu uthenga wabwino okoma. Mzimu Woyera unawasankha iwo kukhala ophunzira a Yesu kudzera mu uthenga wabwino okoma. Tsopano nkhosa zambirimbiri zayamba kulandira Mzimu Woyera ndi kulowa mu mpingo.
Mzimu Woyera unanditsogolera kuti ndiyambe sukulu lautumiki ndi kutukula ophunzira. Iye anadithandiza kuti ndiphunzitse mawu a Mulungu kwa anthu ndi kuwathandiza kuphunzira kumvera mwa chikhulupiliro ndi kutumikira ngati antchito a Mulungu. Analola ntchito ya uthenga wabwino okoma kuchitika kulikonse kumene anali kupita, ndipo Mulungu anadzala mipingo Yake kudzera mwa iwo. Mzimu Woyera wakhala ukutsogolera akapolo Ake kulalikira uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. Mzimu Woyera umatsogolera olungama, amene analandira chikhululukiro cha uchimo, kuti agwirizane ndi mpingo ndi kudalitsidwa kuti akhale ndi moyo olungama m’dziko lino.
Satana wakhala akunyenga anthu kuyambira nthawi yakale ndipo adzapitiliza kuchita choncho. Satana amauza anthu kuti angalandire Mzimu Woyera kudzera mu mapemphero a kulapa, kusala kudya kapena kuika manja. Ichi sichoona konse. Anthu sangalandire Mzimu Woyera kudzera mu mapemphero a kulapa kapena kuika manja. Angalandire Mzimu Woyera pokhapo ngati akhululukidwa machimo awo onse pokhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, umene Mulungu anapereka kwa ife. Ili ndi tanthauzo loona la kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Mzimu Woyera wapitiliza kutsogolera ophunzira a Yesu kuti alalikire uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu kuti athandize anthu kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera.
Mzimu Woyera watitsogolera ife kuti tichite utumiki wazolemba m’dziko lonse lapansi
Monga Paulo analemba uthenga wabwino okoma m’makalata ake, Mzimu Woyera okhala mu mtima mwanga wakhala othandizira kuti ine ndilalikire ndi kufalitsa uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu mu zolemba. Ichi ndi chifukwa chake kuti timasindikiza mabuku a chikristu amene ali ndi uthenga wabwino okoma, amene amatsogolera okhulupirika kukalandira Mzimu Woyera. Poyamba tinayamba ndi timapepala ting’onoting’ono, koma posachedwa mabuku athu amene ali ndi uthenga wabwino okoma ofalitsidwa kuzungulira dziko lonse lapansi.
Mzimu Woyera okhala mwa ine watsogolera anthu ambirimbiri kuti alowe mu mpingo atalandira chikhululukiro cha machimo awo powerenga mabuku ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma. Kuonjezerapo, watitsogolera ife kuti tilalikire uthenga wabwino okoma mu zilankhulo zambiri zakunja. Watitsogolera kuti tilalikire uthenga wabwino okoma pafupifupi ku maiko 150 kuzungulira dziko lonse lapansi, kuphatikizapo United States.
Mzimu Woyera unalimbikitsa mpingo kupempherera utumiki wa dziko lonse ndipo watitsogolera ife kuti timasulire uthenga wabwino okoma zilankhulo zosiyanasina ndi kulalikira kudzera m’mautumiki amabuku kotero kuti anthu ambiri a maiko osiyanasiyana athe kumvera ndi kuukhulupilira. Mzimu Woyera unanditsogolera ine kuti ndigwire ntchito pamodzi ndi atumiki atsopano m’maiko ena ndi kulalikira uthenga wabwino okoma pamodzi nawo kumeneko. Ndikupereka chiyamiko kwa Mzimu Woyera.
Mzimu Woyera unandidzadza ndi chilimbikitso cha kulalikira uthenga wabwino ku Russia. Mzimu Woyera unatitsogolera ife kuti tipemphere ndipo unatipatsa mpata wakuti tikakumane ndi alaliki ofunafuna choonadi a ku Russia ndi kukalalikira uthenga wabwino okoma kwa iwo. Apo ndi pamene iwo inali nthawi yoyamba kumvera uthenga wabwino okoma. Iwo kenako analandira Mzimu Woyera monga ife, atamvera ndi kukhulupilira uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu.
Wina wa iwo, ophunzira kwambiri wa yunivesite ya dziko la ku Moscow, anapereka chibvomerezo chotere kwa ine atamva uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu.
“Ndakhala ndili kukhulupilira mwa Mulungu kwa zaka 6, koma ndinali kukhulupilira kopanda kumumvetsetsa Iye. Komabe, nditamva za uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu, ndinali ndi chikhulupiliro champhamvu ndiponso chitonthozo chodekha mu mtima mwanga. Ndikuyamikadi Ambuye kwambiri. Ndinali ndimaganizo kufikira tsopano pamene ndakhala ndi moyo wachipembezo kudzera mu mtundu wachikhulupiliro choyenera. Moyo wanga wachipembedzo unali ndi chikhulupiliro cha mwazi wa Yesu okha, amene anafa chifukwa cha machimo athu. Komabe, ndinalibe ganizo lililonse kuti Mulungu anayeretsa machimo anga onse.
Kenako ndinakumana ndi abusa obadwa-mwatsopano ndi kumvera za uthenga wabwino okoma umene Mulungu anatipatsa ife, ndipo ndinaphunzira kuti ndinali ochimwabe. Ndinayesa kufufuza zambiri za uthenga wabwino okoma ndiponso za chilungamo kuti chikutanthauza chiani. Ndinazindikira kuti machimo anga onse anaperekedwa kwa Yesu pamene anabatizidwa. Unali uthenga wabwino okoma. Ndinazindikira kuti si uchimo oyamba okha, koma machimonso anga a masiku onse komanso machimo anga a mtsogolo anaperekedwa kwa Iye kudzera mu ubatizo Wake. Ndinapeza chimwemwe chachikulu cha kubadwanso mwatsopano mwa kumvera ndi kukhulupilira mu uthenga wabwinowu wa choonadi.”
A ku Russia ambiri, kuphatikizapo wazamaphunziro kwambiri ameneyu, analandira Mzimu Woyera pokumvera ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. Tsopano mpingo wa Mzimu Woyera unadzalidwa kumeneko. Ndipo anthu ambirimbiri abwera kuzakhulupilira mu uthenga wabwino okoma kudzera mu ntchito ya Mzimu Woyera. Mulungu anachita zinthu zonsezi, ndipo motero ndikupereka chiyamiko kwa Mzimu Woyera.
Mzimu Woyera okhala mwa ine unandipangitsa kukhala Mkristu obadwa-mwatsopano, chimodzimodzi monga iwo onse amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu, ndipo tsopano ndimalalikira uthenga wabwino okoma ku dziko lapansi. Iye walola kuti mabuku athu a uthenga wabwino okoma apitirizebe kutanthauziridwa osati m’Chingerezi chokha, koma mu zilankhulo zinanso zambiri kuzungulira dziko lonse lapansi. Iye anapanga ife kulalikira uthenga wabwino okoma umenewu kuzungulira dziko lonse lapansi. Ndikupereka chiyamiko kwa Mzimu Woyera. Inunso mungalandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Mulungu akufuna inu mukhale ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera.
Anthu ambiri amayesa kulandira Mzimu Woyera mwa kuitana dzina Lake ndi kupereka mapemphero ofunitsitsa kwa Mulungu. Komabe, kuyesa kulandira Mzimu Woyera popanda uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu, umene Yesu anapereka kwa ife, ndi kulakwitsa. Kunena kuti munthu angalandire Mzimu Woyera popanda uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu ndi chiphuzitso chabodza.
Kodi ophunzira a Yesu analandira Mzimu Woyera popanda kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma umene Yesu anapereka kwa iwo? Ai, nzosathekeratu ai. Muyenera kudziwa kuti masiku ano Mzimu Woyera umakhala mwa iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu, ndipo madzi amoyo amayenda mu mitima yawo. Ngakhale pa nthawi ino, madzi amoyo a Mzimu Woyera amatuluka mu mtima mwanga pamodzi ndi uthenga wabwino okoma. Aleluya, Ndikuthokoza Ambuye.