• All e-books and audiobooks on The New Life Mission website are free
  • Explore multilingual sermons in global languages
  • Two new revised editions in English have been released
  • Check out our website translated into 27 languages
Search

Sermons

Mutu 8: Mzimu woyera

[8-9] Uthenga Wabwino wa Ubatizo wa Yesu Umene Watipanga Ife Kukhala Oyera (Aefeso 2:14-22)

Uthenga Wabwino wa Ubatizo wa Yesu Umene Watipanga Ife Kukhala Oyera(Aefeso 2:14-22)
“Pakuti Iye ndi mtendere wathu, amene anacita kuti onse awiri akhale mmodzi, nagumula khoma lakudulitsa pakati, atacotsa udani m’thupi lace, ndiwo mau a cilamulo ca kuchulako malangizo; kuti alenge awiriwa mwa Iye yekha, akhale munthu mmodzi mwatsopano, ndi kucitapo mtendere; ndi kuti akayanjanitse awiriwa ndi Mulungu, m’thupi limodzi mwa mtandawo, atapha nao udaniwo; ndipo m’mene anadza, analalikira Uthenga Wabwino wa mtendere kwa inu akutali, ndi mtendere kwa iwo apafupi; kuti mwa Iye ife tonse awiri tiri nao malowedwe athu kwa Atate, mwa Mzimu mmodzi. Pamenepo ndipo simulinso alendo ndi ogonera, komatu muli a mudzi womwewo wa oyera mtima ndi a banja la Mulungu; omangika pa maziko a atumwi ndi aneneri koma pali Kristu Yesu mwini, mwala wa pangondya; mwa Iye cimango conse, columikizika pamodzi bwino, cikula, cikhale kacisi wopatulika mwa Ambuye; cimene inunso mumangindwamo pamodzi, mukhale cokhalamo Mulungu mwa Mzimu.”
 
 

Mwana otengedwa chifukwa cha umphawi 

 
Kodi n’chiani chinapatula munthu kwa Mulungu?
Uchimo wake ndi umene wachita.

Theka la zaka zana lapita kuyambira pamene nkhondo ya Korea inatha. Koma inasiya zilonda zambiri pakati pa anthu a Korea. Zotsatira zake za Nkhondo ya Korea, ana ambiri anatengedwa kupita nawo ku maiko ena. Ngakhale kuti asilikali a Maiko a Mgwirizano anabwera ku Korea ndi kutithandiza kwakukulu pa nthawi imeneyo, koma ana ambiri anasiidwa opanda atate awo pamene asilikali anachoka. 
Ambiri a asilikali a UN amene anali ndi akazi komanso ana kuno anasiya mabanja awo pamene ankabwerera ku nyumba zawo. Ambiri ana amenewa kenako anasiidwanso ku manyumba osungulako ana ndi amai awo ndipo anaperekedwa kukasungidwa ku maiko ena. Kwenikweni unali mwai kuti anthu achichepere amenewa apeze makolo owathandiza ndi kukula bwino.
Ana otengedwa amenewa anazindikira kuti ankasiyana kwambiri ndi makolo awo ndiponso oyandikana nawo pamene iwo ankakula, ndipo anaphunzira kuti anatengedwa ku dziko lakutali lotchedwa Korea. ‘Kodi n’chifukwa chiani makolo anga anandisiya ine?’ Kodi ananditumiza ine ku dziko lino chifukwa anandida ine?’ Ndi maganizo awo achibwana, ana amenewa sankamvetsetsa zimene zinali kuchitika. 
Chidwi chawo ndiponso udani wao kwa makolo awo unayamba kukula mogwirizana ndi khumbo lofuna kukumana nawo. ‘Sindikudziwa m’mene makolo anga amaonekera? Kodi iwo anandisiiranji ine? Kodi anachita choncho chifukwa anali kundida? Ai, payenera kuti panali chifukwa chimene anachitira zimenezi.’ Mwina panali kusamvetsetsana ndipo nthawi zina ankamva udani. Ndipo nthawi zina mwina sankafuna kuti aganizenso za zimenezo. Asanadziwe ngakhale za zimenezi, nthawi inapita ndipo ana anakula kukhala achikulire. Anakwatira, ndi kukhala ndi ana ndi kupanga mabanja a iwo okha. 
Ndinakhala ndi chidwi ndi anawa kudzera mu pulogalamu ya Kanema ina yakomweko. Mu pulogalamu imeneyi, mtola nkhani wa Kanema anafunsa mkazi amene tsopano akukhala ku German amene anatengedwa. Mkazi ameneyu anali mu zaka za m’makumi awiri pa nthawi imeneyo ndipo anali kuphunzira zaumulungu. Poyamba, mkazi ameneyu anayesa kwambiri kuzemba kuti asakumane ndi atola nkhani chifukwa sanali kufuna aliyense kuti adziwe kuti anali otengedwa. Mtola nkhani anamunyengerera iye kuti amvetsetse kuti kuzipereka mu m’mafuso ake kuzamuthandiza kuzindikira chimene anatengedwera kumaiko ena. Mkaziyo anavomera. 
Limodzi la mafunso a mtola nkhani linali lakuti, “Kodi unganene chiani utakhala kuti wakumana ndi makolo ako enieni? Kodi uli ndi chidwi chofuna kudziwa chiani?” Mkaziyo anayankha kuti, “Sindikumvetsetsa chifukwa chomwe iwo anadiperekera kuti ndisungidwe. Ndikanakonda kuwafunsa iwo ngati anandida ine.” Amai ake omubereka anaona mkaziyo pa Kanema akufunsidwa mafunso, analumikizana ndi nyumba youlutsira mau, ndikunena kuti akufuna kukumana ndi mwana wake wamkazi. Umu ndi m’mene awiriwa anakumanirana. 
Amai ake analawira m’mawa kubwalo la ndege ndi kuyembekezera kubwera kwa mwana wake wamkazi wao. Pamene mkazi wachichepere anatuluka pakhomo, amai ake anangoima potero ndikumalira. 
Anthu awiriwa sanakumanepo maso ndi maso. Nthawi yoyamba imene mai anaona mwana wake wamkazi wamkulu ndipamene anaoneka pa Kanema. Ngakhale kuti anali kuyankhula zilankhulo zosiyana anali kutha kuyankhulana m’mitima yawo, ndipo kudzera m’mayang’anidwe wokhudzika anali kusinthana. Anagwirana nkhope wina ndi mzake pamene maiyo anali kupempha chikhululukiro pa zimene anachita. Chomwe ankachita ndi kulira basi ndi kubwereza kuti anali olakwa. 
Amai ake anabweretsa mwana wawo kunyumba ndipo anadya naye pamodzi. Komabe, mwana wamkazi anali kulankhula Chigermani chokha ndipo amai ake anali kulankhula kokha Chikorea, Choncho sanathe kumvetsetsana mu kayankhulidwe. Koma mwina mwake pa choona chakuti anali amai ndi mwana zinawalola kuti athe kumvetsetsana. Anali ndi zokambirana zopanda mawu zambiri ndipo ankazionetsera kudzera mu zizindikilo, kugwirana nkhope wina ndi mnzake ndi kulankhula kugwiritsa ntchito maso ndi mitima yawo. 
Pa nthawi imene anabwerera ku German, mwana wamkazi anadziwa kuti amai ake omubereka anali kumukonda. Atolankhani omwewa analumukizana naye m’mafunso oyamba analankhulana nayenso asanachoke. “Panalibe kufunika koti ndifunse cholinga chimene amai anga anandipereka kuti ndikasungidwe. Amai anga ndi osauka ngakhale tsopano. Anthu olemera m’dziko lino ndi achuma kwambiri kotero kuti amayendetsa magalimoto akunja, koma amai anga akukhalabe muumphawi.” Iye anapitiriza kunena kuti, “Ngakhale kuti sindinawafunse amai anga funso limenelo ndi kusalandila yankho kuchokera kwa iwo, ndinaona kuti ananditumiza kutali kotero kuti andipulumutse kuumphawi. Ndi chifukwa chake sindinafunike kuwafunsa funso limenelo, ndiponso chifukwa chimene kukaika konse ndi kudana tsopano zachoka.” 
 
 

Anthu amapatulidwa kwa Mulungu chifukwa cha uchimo m’mitima yawo 


Kodi n’chifukwa chiyani tikukhala opatulidwa ndi Mulungu, ndipo ndi chifukwa chiyani sitibwera pafupi ndi Iye? Mkazi amene anaikidwa kwa omusunga anaphunzira kuti amai ake omubereka anamtumiza kutali pofuna kumpulumutsa ku umphawi. Kodi ndi chimodzimodzi ndi choona cha Mulungu? Mulungu anatilenga ife m’chifaniziro Chake. Kodi ndi chiani chimene chikanatilekanitsa ndi Iye? Yankho ndi lakuti Satana anayesa munthu kuti achite tchimo, ndipo tchimo linalekanitsa munthu kwa Mulungu. 
Pachiyambi, Mulungu analenga munthu m’chifaniziro Chake ndipo anakonda chilengedwe Chake kwambiri. Anthu analengedwa ngati chikhazikitso cha chikondi cha Mulungu ndipo anali ndi ulemelero ochuruka kuposa zolengedwa zina zonse. Komabe, Mngelo wakugwa otchedwa Satana anagwira ntchito yolekanitsa munthu kwa Mulungu. Satana anayesa munthu kuti asakhulupilire mau a Mulungu, ndipo anamupangitsa iye kuti adye chipatso cha mtengo opatsa nzeru zabwino ndi zoipa. 
Munthu motero analekana ndi Mulungu chifukwa cha uchimo wake. Munthu anali osamvera kwa Mulungu. Munthu sanadye chipatso cha mtengo wa moyo, umene umapatsa moyo osatha ndipo umene Mulungu analola, koma m’malo mwake anadya chipatso choletsedwa chimene chinamupatsa iye nzeru zodziwa chabwino ndi choipa. Zotsatira zake zinali zakuti munthu anapatulidwa kwa Mulungu. 
posachedwapa chithu cha chikondi cha Mulungu, munthu sanamvere ndipo anakhala opatulika kwa Iye chifukwa cha mwano wake. Chifukwa cha uchimo umene unadza kukhala mu mtima mwake, munthu pamenepo anapatulidwa kwa Mulungu. Kuchoka apo, munthu anakhala kutali ndi Mulungu kwa nthawi yaitala ndi kumadandaula, “Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu anatisiya ife atatipanga ife? Kodi n’chifukwa chiyani Iye anatilola ife kuti tichite tchimo? Kodi n’chifukwa chiyani amatipereka ku Gahena pamene anatipanga ife wofooka? Kukanakhala bwino kukanakhala kuti sanatipange ife poyamba.” Tinkakhala ndi mafunso ambiri, ndiponso achidwi, zikaiko ndiponso udani tisanabadwe mwatsopano. 
Pamene ndinaona mkazi otengedwa pa pulogalamu ya pa Kanema, ndinazindikira kuti ubale pakati pa munthu ndi Mulungu ndi chimodzimodzi ndi ubale umene anali nawo kwa amai ake enieni. Palibe chisautso, kusamvetsetsana, tembelero kapena uchimo wa mtundu ulionse zikanasiyanitse munthu kwa Mulungu m’nyengo ziliyonse. Ndiponso, ndinatha kumvetsa kuti ngakhale kuti ubale pakati pa Mulungu ndi munthu umachokera pa chikondi, kunali kothekabe kuti kumvetsetsana kuchitike. 
Monga m’mene amai sanapereke kutali mwana wake wamkazi chifukwa cha udani, choncho Mulungu anadzilekanitsa yekha kwa munthu osati chifukwa cha udani koma chifukwa cha uchimo. Palibe chifukwa choti Mulungu adane ndi munthu ndipo palibe chifukwa choti anthu adane ndi Mulungu. Timakondana wina ndi mzake. Chifukwa chimene munthu amakhalabe opatukana ndi Mulungu ndi chakuti munthu anakhala ochimwa atagonjera mabodza a Satana. 
 

Mulungu anatikumbatira ife kudzera mwa Yesu 

“Koma tsopano mwa Yesu Kristu inu amene munali kutali kale, anakusendezani mukhale pafupi m’mwazi wa Kristu. Pakuti Iye ndi mtendere wathu, amene anacita kuti onse awiri akhale mmodzi, nagumula khoma lakudulitsa pakati, atacotsa udani m’thupi lace, ndiwo mau a cilamulo ca kuchulako malangizo; kuti alenge awiriwa mwa Iye yekha, akhale munthu mmodzi mwatsopano, ndi kucitapo mtendere.” (Aefeso 2:13-15). Ambuye anabatizidwa ndi Yohane ndi kuchotsa machimo onse a dziko pofuna kuti achotse lamulo la malangizo. Iye kenako anakhetsa mwazi Wake pa Mtanda kuti apulumutse munthu ku machimo ake ndi kumulola iye kuti akumbatilidwe ndi Mulungu. Mulungu tsopano wakumbatira iwo amene anayeretsedwa ndi Iye.
Kodi munaganizirapo za dziko lopanda madzi? Osati kale kwambiri, ndinapezekapo pa msonkhano ophunzira Baibulo ku mnzinda wa Inchoni, limodzi mwa madoko aakuluakulu mu Korea kumene madzi aku pompi sanagwire ntchito nthawi imeneyo kwa masiku ochepa ndipo ndinganiza kuti, ‘Anthu sangakhale opanda madzi.’ 
Ngati Mulungu angapange dzikoli kukhala lopanda madzi kwa mwezi umodzi, kungakhale kosatheka kukhala m’mizinda chifukwa cha fungo loipa, zonyansa ndiponso ludzu ponseponse. Tiyenera kumvetsetsa kufunika kwa madzi, amene Mulungu anatipatsa ife. Monga madzi ali ofunikira kwambiri kwa anthu, ubatizo umene Yesu analandira kwa Yohane mu Mtsinje wa Yordano ndi ofunikiranso chimodzimodzi. 
Kukanakhala kuti Yesu sanabwere padzikoli ndi kubatizidwa ndi Yohane, ndiye kodi okhulupilira mwa Yesu anakalandira bwanji chikhululukiro cha machimo? Monga anthu amene sangathe kukhala popanda madzi, aliyense mu dziko lino akanafa ku machimo awo kukanakhala kuti Yohane sanabatize Yesu. 
Komabe, popeza ubatizo wa Yesu unachotsa machimo athu onse, tsopano tingathe kumva chilimbikitso mu nzeru yakuti mitima yathu inayeretsedwa ndipo tinadalitsidwa ndi chipulumutso. Ubatizo wa Yesu ndi ofunikira ku chikhulupiliro chathu. Kuonjezerapo, ubatizo Wake ndi ofunikira kwambiri kuti ife tilandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera. 
Petro, m’modzi wa ophunzira wa Yesu anati, “Cimenenso cifaniziro cace cikupulumutsani tsopano, ndico - ubatizo, mwa kuuka kwa Yesu Kristu.” (1 Petro 3:21). Mfundo ya Petro imanena kuti Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi, ndi kukhetsa mwazi Wake kotero kuti apulumutse ife ku machimo athu. Ubatizo wa Yesu, umene unatsuka machimo onse a dziko, ndi uthenga wabwino oona. 
Tsopano tiyeni tione ndime imene ikunena za mkhate wamkuwa yorembedwa mu Eksodo 30:17-21. “Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, ndi kuti, Upangenso mkhate wamkuwa, ndi tsinde lace lamkuwa, wakusambiramo; nuuike pakati pa cihema cokomanako ndi guwa la nsembe, ndi kuthiramo madzi. Ndipo Aroni ndi ana ace amuna azisamiramo manja ao ndi mapazi ao; pakulowa iwo m’cihema cokomanako asambe ndi madzi, kuti angafe; kapena poyandikiza guwa la nsembe kutumikirako, kufukiza nsembe yamoto ya Yehova; asambe manja ao ndi mapazi ao, kuti angafe: liwakhalire lemba losatha kwa iye ndi kwa mbeu zace, mwa mibadwo yao.”
Mu chihema munali mkhate wamkuwa, umene unaikidwa pakati pa chihema chokumanako ndi pa guwa, m’mene munali madzi osamba m’manja. Kukanakhala kuti mkhate umenewu sunali mu chihema, ansembe opereka nsembe akanakhala ndi litsiro lotani . 
Kodi mwazi ndi litsiro zikanadetsa motani a ansembe amene anali kupereka nsembe za anthu masiku onse ndi kuika manja pa nsembe zauchimo ndipo kenako kuzipha? Kukanakha kuti munalibe mkhate mu chihema, ansembe akanakhala ndi litsiro kwambiri. 
Ichi ndi chifukwa chake Mulungu anakonza mkhate kwa iwo kuti afike pafupi ndi Iye ali ndi manja aukhondo. Ochimwa ankapereka machimo awo poika manja pa mutu pa nsembe zauchimo, ndipo kenako wansembe anali kuzipereka kwa Mulungu m’malo mwa iwo. Mulungu anakonza mkhate wamkuwa ndi cholinga choti ansembe azilowa m’malo opatulika, ndipo choncho anali kusamba ndi madzi, kuopa kuti angafe. Ngakhale wansembe sakanalowa m’malo oyera ali ndi litsiro la mwazi wa nyama. Ndi chifukwa chake wansembe anali kusamba litsiro lake lonse ndi madzi a mu mkhate kotero kuti afike pafupi ndi Mulungu atapereka nsembe za anthu. 
 
 

Ubatizo wa Yesu unatsuka machimo onse adziko 


Kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi Yohane mu Mtsinje wa Yordano, machimo onse adziko anaperekedwa kwa Iye. Ndipo kumizidwa Kwake kotheratu m’madzi kukusonyeza imfa Yake ndipo kuturuka Kwake m’madzi kukuimira kuukanso Kwake. M’mawu ena, Yesu anabatizidwa ndi Yohane kuti anyamule uchimo onse wa dziko, kulipira mphoto yonse yauchimo ndi kufa pa Mtanda. Imfa Yake inali kulipira malipiro a machimo athu ndipo kuukanso Kwake kunatipatsa ife moyo osatha. 
Ngati sitinakhulupilire kuti Yesu anachotsa machimo athu onse kudzera mu ubatizo Wake, mitima yathu ikanakhala yodzala ndi uchimo. Motero, kodi tikanatha kuyandikira bwanji kwa Mulungu? Uthenga wabwino wa chikhululukiro cha machimo sichiphunzitso cha chipembezo chimodzi koma choonadi cha Mulungu. 
Sitingakhale ndi chikhulupiliro chathu kopanda nzeru yangwiro, m’mawu ena, sitingagonjetse dziko ngati sitisamaladi zoti Yesu anabatizidwa ndi Yohane. Monga m’mene zamoyo zonse zimafunika madzi kotero kuti zisamalire miyoyo yawo, tikufunika chikhululukiro cha machimo ndi madzi a ubatizo wa Yesu kuti tikhale ndi chikhulupiliro ndi kulowa mu Ufumu wa Kumwamba. Yesu anafunikira kubatizidwa, kufa pa Mtanda ndi kuukanso kuti atipulumutse ife ku machimo athu onse. Uwu ndi uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, umene tiyenera kukhulupiliramo ndi mitima yathu yonse. 
Ngakhale kuti Yesu anapachikidwa kufikira kufa pa Mtanda, Iye sanachite chiri chonse choyenera chilango chotere. Iye anabwera padziko lino kuzatsuka machimo athu, anabatizidwa ali ndi zaka 30, ndipo anakhala Mpulumutsi wathu kudzera mu imfa Yake ya pa Mtanda ali ndi zaka 33. Mulungu anafuna kupanga mtundu wa anthu kukhala ana Ake posatengera kuti tinali ofoka ndiponso ochimwa motani. Ndi chifukwa chake Yesu anabatizidwa. Mulungu anatipatsa ife chikhululukiro cha machimo ndi mphatso ya Mzimu Woyera pa nthawi imodzi. 
Baibulo limanena kuti ngati munthu sabadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kuona Ufumu wa Mulungu kapena kulowamo (Yohane 3:3-5). Muyenera kudziwa ndi kukhulupilira kuti Yesu anabatizidwa kuti atsuke machimo athu onse. Ngakhale kuti munthu ndi Mkristu obadwa-mwatsopano, ngati sanasinkhesikhe pa choonadi kuti Yesu Kristu anachotsa machimo a dziko kudzera mu ubatizo Wake, mtima wake uzakhala walitsiro posachedwapa. Chifukwa ndife akuthupi, ndife oyenera kukhala ndi litsiro lauchimo ngakhale mu moyo wathu wa masiku onse. Ndi chifukwa chake tifunika nthawi zonse kukhala mwa chikhulupiliro, kulingalira za ubatizo wa Yesu, mwazi Wake, ndi kuukanso Kwake. Chikhulupiliro chimenechi chimatisunga ife kufikira tsiku lomwe tidzalowe mu Ufumu wa Kumwamba. 
Yesu analibe chisankho koma kubatizidwa ndi kufa chifukwa cha machimo athu, choncho tiyenera kukhulupilira kuti pochita choncho anatibweretsera ife chipulumutso. Palibe zambiri zimene tiyenera kuchita kuposa kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma kuti tiomboledwe ku machimo onse a dziko lapansi. 
Tikupereka mathokozo kwa Ambuye, amene anatipatsa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Mphatso yaikulu imene Mulungu anapereka ndi kutumiza Mwana Wake obadwa Yekha kudzatipulumutsa ife ku machimo athu kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi. 
Chifukwa chimene sitikanayandikirana ndi Mulungu ndipo tinakakamizidwa kukhala kutali ndi Iye chinali chakuti tinali ndi uchimo m’mitima yathu. Yesu anabatizidwa ndi Yohane kuti achotse machimo onse adziko ndi kufa pa Mtanda kuti agumule khoma limene linalekanitsa Mulungu ndi munthu. Ubwenzi pakati pa Mulungu ndi munthu unabwezeretsedwa ndi ubatizo Wake ndiponso mwazi. Tikumuyamika chifukwa cha mphatso zimenezi. Chikondi cha makolo akuthupi ku mwana wawo ndi chachikulu, koma ndi chosafanana ndi chikondi cha Mulungu, chimene Yesu anatipulumutsira ife ochimwa. 
Ubatizo wa Yesu ndi mwazi zonse ndi zofunikira. Kukanakhala kuti kunalibe madzi kudziko lino, kodi chamoyo chilichonse chikanapulumuka? Popanda ubatizo wa Yesu, sikukanakhala wina wake opanda tchimo mu mtima wake. Kukanakhala kuti Yesu sanabatizidwe ndipo akanakhala kuti sanafe pa Mtanda, panalibe amene akanalandira chikhululukiro cha machimo. Mwa mwayi, Yesu anabatizidwa ndipo anapanga nsembe yokwanira kwa ife. Ngakhale kuti tikusoweka ndiponso kulakwitsa, tingalandire Mzimu Woyera pokhulupilira mu ubatizo Wake ndi mwazi wa pa Mtanda. 
Anthu amene amakhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi imfa ya pa Mtanda angayandikire pafupi ndi Mulungu, kupemphera ndi kumutamanda. Tsopano tikutha kutamanda Ambuye ndi kumupembeza chifukwa takhala ana Ake. Ichi ndi chisomo cha Mulungu komanso dalitso. Uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda ndi odabwitsadi. Tingathe tonse kulandira chipulumutso ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera mwa kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma umenewu.