• All e-books and audiobooks on The New Life Mission website are free
  • Explore multilingual sermons in global languages
  • Two new revised editions in English have been released
  • Check out our website translated into 27 languages
Search

Sermons

Mutu 8: Mzimu woyera

[8-10] Yendani mu Mzimu! (Agalatiya 5:16-26, 6:6-18) 

Yendani mu Mzimu!(Agalatiya 5:16-26, 6:6-18) 
“Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse cilakolako ca thupi. Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazicite. Ngati Mzimu akutsogolerani, simuli omvera lamulo. Ndipo nchito za thupi zionekera, ndizo dama, codetsa, kukhumba zonyansa, kupembedza mafano, nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko, njiru, kuledzera, mcezo, ndi zina zotere; zimene ndikucenjezani nazo, monga ndacita, kuti iwo akucita cita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu. Koma cipatso ca Mzimu ndico cikondi, cimwemwe, mtendere, kuleza mtima, cifundo, kukoma mtima, cikhulupiriro, cifatso, ciletso; pokana zimenezi palibe lamulo. Koma iwo a Kristu Yesu adapacika thupi, ndi zokhumba zace, ndi zilakolako zace. Ngati tiri ndi moyo ndi Mzimu, ndi Mzimunso tiyende. Tisakhale odzikuza, outsana, akucitirana njiru.”
“Komai iye amene aphunzira mau ayenera kucereza wophunzitsayo m’zonse zabwino. Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti cimene munthu acifesa, cimenenso adzacituta. Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, cocokera m’thupi adzatuta cibvundi; koma wakufesera kwa Mzimu, cocokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha. Koma tisaleme pakucita zabwino; pakuti pa nyengo yace tidzatuta tikapanda kufoka. Cifukwa cace, monga tiri nayo nyengo, ticitire onse cokoma, koma makamaka iwo a pa banja la cikhulupiriro. Taonani, malembedwe akuruwo ndakulemberani inu ndi dzanja langa la ine mwini. Onse amene afuna kuonekera okoma m’thupi, iwowo akukangamizani inu mudulidwe; cokhaco, cakuti angazunzike cifukwa ca mtanda wa Kristu. Pakuti angakhale iwo omwe odulidwa sasunga lamulo; komatu afuna inu mudulidwe, kuti akadzitamandire m’thupi lanu. Koma kudzitamandira ine konse konse, iai, koma mu mtanda wa Ambuye wathu Yesu Kristu, amene mwa Iye dziko lapansi lapacikidwira ine, ndi ine ndapacikidwira dziko lapansi. Pakuti mdulidwe ulibe kanthu, kusadulidwa kulibe kanthunso, komatu wolengedwa watsopano. Ndipo onse amene atsata cilangizo ici, mtendere ndi cifundo zikhale pa iwo, ndi pa Israyeli wa Mulungu. Kuyambira tsopano kulibe munthu andibvute, pakuti ndiri nayo ine m’thupi mwanga mikwingwirima ya Yesu. Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu cikhale ndi mzimu wanu, abale. Amen.”
 

Kodi tiyenera kuchita chiani kuti tiyende mu Mzimu?
Tiyenera kulalikira ndi kutsatira uthenga wabwino okoma.

Mtumwi Paulo analemba za Mzimu Woyera mu kalata yake ya ku Agalatiya. Mu Agalatiya 5:13-14 iye anati, “Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; cokhaco musacite nao mfulu wanu cothandizira thupi, komatu mwa cikondi citiranani ukapolo. Pakuti mau amodzi akwaniritsa cilamulo conse ndiwo; Uzikonda mnzako monga uzikonda iwe mwini.” 
Mwachidule, uthenga ndi wakuti popeza tinamasulidwa ku uchimo pokhulupilira mu uthenga wabwino okoma, sitiyenera kutenga ufulu umenewu ngati mpata woziika tokha mu zilakolako za thupi, koma kudzera mu chikondi tiyenera kutumukirana wina ndi mnzake ndi kutsatira uthenga wabwino okoma. Monga Mulungu watipulumutsa ku machimo athu onse, ndi koyenera kwa ife kulalikira uthenga wabwino. Paulo nayenso ananena kuti, “Koma ngati mulumana ndi kudyana, cenjerani mungaonongane” (Agalatiya 5:15).
 
 

Yendani mu Mzimu kuti mudzadzidwe ndi Mzimu Woyera 


Mu Agalatiya 5:16 Paulo ananena kuti “Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse cilakolako ca thupi.” Ndipo mu ndime 22-26 anati, “Koma cipatso ca Mzimu ndico cikondi, cimwemwe, mtendere, kuleza mtima, cifundo, kukoma mtima, cikhulupiriro, cifatso, ciletso; pokana zimenezi palibe lamulo. Koma iwo a Kristu Yesu adapacika thupi, ndi zokhumba zace, ndi zilakolako zace. Ngati tiri ndi moyo ndi Mzimu, ndi Mzimunso tiyende. Tisakhale odzikuza, outsana, akucitirana njiru.” Apa, Paulo akutiuza kuti ngati tingayende mu Mzimu, tizabala chipatso cha Mzimu. Mzimu Woyera umafuna kuti ife tidziyenda mu Mzimu. Koma timakhala m’thupi. 
Ife anthu timabadwa ndi thupi limene silingabale chipatso cha Mzimu. Ngakhale kuti tingayese kuyenda mu Mzimu, chibadwidwe chathu sichingasinthe. Ndi chifukwa chake okhawo amene alandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera mu uthenga wabwino okoma ndi amene angayende mu Mzimu ndi kubala chipatso cha Mzimu. 
Pamene Baibulo likutiuza ife kuti tiyende mu Mzimu, likutanthauza kuti tiyenera kulalikira uthenga wabwino okoma kuti ena akhululukidwenso machimo awo. Ngati tidzakhala chifukwa cha uthenga wabwino umenewu, tizabala chipatso cha Mzimu. M’mawu ena, sinkhani yosintha chibadwidwe cha munthu. Pamene tikuyenda ndi uthenga wabwino okoma umenewu, tingabale chipatso cha Mzimu, monga chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso komanso chiletso. Chipatso cha Mzimu chimatithandiza ife kupulumutsa ena ku machimo awo kuti akhale ndi miyoyo yosatha. 
 
 

Zilakolako za thupi ndi zokhumba za Mzimu 


Paulo anati, “Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazicite.” (Agalatiya 5:17). Popeza ife, amene taomboledwa, tili ndi zilakolako za thupi ndi za Mzimu pa nthawi imodzi, zinthu ziwiri zimenezi nthawi zonse zimalimbana wina ndi mnzake. Zotsatira zake ndi zakuti palibe chimodzi cha izo chingakhutilitse kwathunthu mitima yathu.
Mzimu umatitsogolera ku chifuno, kuchokera pansi pa mitima yathu, kuti tilalikire uthenga wabwino okoma ndi kutumikira Ambuye. Umatipangitsa kufunitsitsa kuziika mu ntchito za uzimu. Umatithandiza kupulumutsa anthu ku machimo awo polalikira uthenga wabwino okoma wa Mulungu. 
Koma kumbali ina, zokhumba zathu zimautsa zilakolako zathupi n’cholinga choti tisayende mu Mzimu. Uwu ndi nkangano pakati pa Mzimu ndi zilakolako za thupi. Ngati munthu watengedwa ndi zilakolako za thupi, iye pomaliza amachita zofuna za thupi. Thupi limaika chilakolako chake molimbana ndi Mzimu. Zimatsutsana otsutsana wina ndi mnzake, ndi cholinga choti tisachite zinthu zimene tikufuna. 
Nanga kodi kuyenda ndi Yesu kumafunika chiani? Ndipo ndi zinthu zotani zimene zimakondweretsa Mulungu? Mulungu anati kulalikira ndi kutsatira uthenga wabwino okoma ndiye moyo woyenda mu Mzimu. Iye amapereka mitima ya kuyenda mu Mzimu kwa iwo amene ali ndi kukhazikika kwa ndi Mzimu Woyera, pofuna kuti akhale ndi moyo wauzimu. Lamulo limene Mulungu anatipatsa kuti tibale chipatso cha Mzimu mwa kuyenda mu Mzimu linali chenjezo ndiponso lamulo kwa ife kuti tipulumutse ena ku machimo awo polalikira uthenga wabwino okoma. Kuyenda mu Mzimu Woyera kukutanthauza kukhala mu moyo umene umakondweretsa Mulungu. 
Kuti tiyende mu Mzimu, tiyenera kukhala ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera choyamba pa zonse. Tiyenera choyamba kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma umene Mulungu anapereka kwa ife ngati tikufuna kulandira Mzimu Woyera umene umakhala mwa ife. Ngati sitikhulupilira mu uthenga wabwino pansi pa mitima yathu, sitizalandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera kapena kupeza chipulumutso cha uchimo, kutanthauza kuti sitizakwanitsa kuyenda mu Mzimu. 
Mzimu Umatipatsa khumbo la kulalikira uthenga wabwino okoma, kutumikira Ambuye ndi kubweretsa ulemelero kwa Mulungu. Khumbo limeneli lichokera mu mtima umene uli ozipereka kwa Mulungu ndi kulalikira uthenga wabwino okoma ku dziko lonse lapansi. Limachokeranso mu mtima umene umafunitsitsa kuchita chilichonse chothekera kuti ulalikire uthenga wabwino okoma. Iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma ndi kulandira Mzimu Woyera atakhululukidwa machimo awo angathe kuyenda mu Mzimu ndi kuzipereka okha kulalikira uthenga wabwino. Ichi ndiye cholowa chawo chochokera kumwamba.
Iwo amene ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera amamvera Mzimu Woyera ndi kuyenda mu Mzimu, ngakhale kuti adakali ndi zilakolako za thupi chifukwa Mzimu umakhala mwa iwo. Paulo anati, “Yendani mu Mzimu.” Chimene anatanthauza ndi chakuti tiyenera kulalikira uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu Woyera umene Yesu anapereka kwa ife kotero kuti tithandize ena kuti akhululukidwe ku machimo awo. 
Nthawi zina pamene tikuyenda mu Mzimu, timayenda mogwirizana ndi thupi. Chilakolako cha thupi ndi chokhumba cha Mzimu zimamenyana wina ndi mzake mu miyoyo yathu, koma chimene tiyenera kudziwa ndi kuzindikira momveka bwino ndi chakuti iwo amene ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera ayenera kukhala ndi moyo oyenda mu Mzimu. Pokhapo mwa njira imeneyi ndipomwe tizatha kukhala odzadzidwa ndi madalitso a Mulunga. Ngati iwo amene ali ndi kukhazikika ndi Mzimu Woyera akunyalanyaza kubala chipatso cha Mzimu, adzaonongedwa chifukwa cha kubala chipatso chathupi. Chipatso chawo ndi chobvunda komanso chomvetsa chisoni. Motero pali chifukwa chimene ife tiyenera kukhalira poyendera mu Mzimu. 
Tinamva kuti “Yendani mu Mzimu,” koma ena mwa ife tingaganize kuti “Kodi ndingachite bwanji zimenezo, pamene sindikumva Mzimu Woyera mkati mwanga?” Ena a ife tingaganiza kuti tingazindikire kukhazikika kwa Mzimu Woyera pokhapo ngati Mulungu waonekera ndi kulankhula nafe mwachindunji. Koma chimenechi ndi chosamvetsetseka. Mzimu umatipatsa khumbo lokhala mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. 
Pangakhalenso nthawi zina pamene tingatsimikize kuti Uwo umakhala mkati mwathu koma sitingaumve chifukwa timayenda mogwirizana ndi thupi. Ena angaganizenso kuti Uwo ukugona mkati mwathu. Iwo ndi amene alandira Mzimu Woyera koma adakali kuyenda mwa kuthupi. 
Anthu amenewa amatonthoza thupi lawo lokha ndi kuchita m’mene likunenera koma amavutika pamapeto chifukwa cha zinthu zimene thupi lawo limafuna. Ngakhale iwo amene ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera amatha kukhala mogwirizana ndi zilakolako za thupi lawo, chifukwa amaganiza kuti ndi chibadwe kuchita zimenezo. Koma iwo amene amadzipereka okha ku thupi pamapeto pake amakhala akapolo a thupi. 
Ambuye akutiuza kuti tikhale mogwirizana ndi Mzimu. Ichi chikutanthauza kutumikira uthenga wabwino okoma. Chikutanthauzanso kuti tiyenera kudzipereka tokha kwathunthu ku uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. Kusangalala mu uthenga wabwino ndi kukhala mwa iwo ndi kukhala mogwirizana ndi Mzimu. Tiyenera kukhala motero pophunzira chimene chikutanthauza kuyenda mu Mzimu. Kodi mukuyenda mu Mzimu? 
 
 

Kodi munthu amene alibe kukhazikika kwa Mzimu Woyera angayende mu Mzimu? 


Iwo amene sanabadwe mwatsopano sakudziwa chimene chikutanthauza kuyenda mu Mzimu. Motero, anthu ambiri amayesa kulandira Mzimu Woyera ndi kufunitsitsa Uwo m’njira yawo. Amaganiza kuti ntchito ya kukhumba Mzimu Woyera ndi chimodzimodzi ndi kudzadzidwa ndi Mzimu Woyera. 
Mwachitsanzo, pamene anthu asonkhana mu mipingo ina kuti achite mapemphero, mtumiki amapemphera mokweza ndipo aliyense amayamba kulira akutchula dzina la Ambuye. Ena a iwo amayankhula m’malilime ngati kuti adzadzidwa ndi Mzimu Woyera, koma palibe ndi m’modzi yemwe, osati ngakhale iwo eni, angathe kumvetsetsa zimene akunena. mosachedwa, ena a iwo amagwa pansi ndipo matupi awo amayamba kunjenjemera m’chimwemwe. Iwo mwachidziwikire amakhala ndi ziwanda koma amaganiza kuti alandira Mzimu Woyera. Ndiyeno kumabwera phokoso pamene anthu afuula mokweza, “Ambuye, Ambuye!” Amaitana Ambuye, kukhetsa misozi ndi kumomba m’manja. Chinthu chotere chimatchedwa kuti “kudzadzidwa ndi Mzimu Woyera.” 
Mtumiki amayankhula m’malilime kwinaku akumenya guwa, ndipo anthu amafuula mokweza, “Ambuye! Ambuye!” Amakonda malo otere ndipo ngakhale ena amanena kuti aona masomphenya a mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa m’munda wa Edeni ndi nkhope ya Yesu pamene anali kukomoka ndi mapemphero osalungama. Iwo amalakwitsa zimenezo ngati njira zolandilira Mzimu Woyera, kudzadzidwa ndi Iye ndi kuyenda ndi Iye. Zochita zawo zosochera zimadzetsa kusamvetsetsa za mawu a Mulungu ndi Mzimu Woyera. 
“Kuyenda mu Mzimu.” Ichi ndi chimene Mulungu amanena kwa iwo amene abadwa mwatsopano. Zikutanthauza kuti kuchita zinthu zimene zimakondweretsa Iye. Paulo anasiyanitsa zochita zathupi ndi chipatso cha Mzimu Woyera. Iye anati “Koma cipatso ca Mzimu ndico cikondi, cimwemwe, mtendere, kuleza mtima, cifundo, kukoma mtima, cikhulupiriro, cifatso, ciletso” (Agalatiya 5:22-23). 
“Kuyenda mu Mzimu” kukutanthuza kulalikira uthenga wabwino okoma ndi kupulumutsa ena ku machimo awo. Ngati tichita choncho, tizakwanitsa kubala chipatso cha Mzimu. Zipatso za Mzimu ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso komanso chiletso, ndipo tizakwanitsa kubala chipatso chimenechi pokhapo ngati tikhala mwa uthenga wabwino okoma. Ngati munthu akutumikira ndi kulalikira uthenga wabwino okoma, kuzipereka nsembe yekha chifukwa cha uwo, ndiyeno adzatha kukhala ndi moyo wauzimu odzala ndi Mzimu Woyera. 
Monga chipatso cha Mzimu, “kukoma mtima” kukutanthauza kuchita ntchito zabwino. Zikutanthauzanso ukoma. Kusunga ukoma chifukwa cha uthenga wabwino okoma ndi kuchita chinthu chopindulitsa ena ndi ubwino. Chabwino chopambana pamaso pa Mulungu ndi kulalikira uthenga wabwino popindulitsa ena. 
Ndipo “chifundo” ndi kumva chisoni kwa anthu. Iye amene ndi wachisomo kwa ena amatumikira uthenga wabwino ndi chipiliro komanso chifundo adzakhala pamtendere. Iye amene amayenda mu Mzimu ndi okondwa kuona ntchito ya Mulungu ikukwaniritsidwa, amakonda kuchita ntchito Yake, amakonda ena ndipo ndi okhulupirika mu zinthu zonse. Ngakhale palibe amene anapereka chikakamizo chochita zimenezo, iye amene ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera ndi okhulupirika mu ntchito Yake kufikira itakwaniritsidwa. Iye ndi ofatsa ndipo akusungabe kudziletsa. Iye ali ndi chipatso cha Mzimu. Munthu amene ali ndi Mzimu Woyera mwa iye ayenera kuyenda mu Mzimu. Pokhapo ngati achita zimenezi, ndi pomwe iye adzakwanitsa kubala chipatso cha Mzimu. 
Mungabalenso chipatso cha Mzimu ngati mukuyenda mu Mzimu. Koma ngati simukuchita zimenezo, muzayenda mu zilakolako za thupi. Malemba anena kuti mu Agalatiya 5:19-21, “Ndipo nchito za thupi zionekera, ndizo dama, codetsa, kukhumba zonyansa, kupembedza mafano, nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko, njiru, kuledzera, mcezo, ndi zina zotere; zimene ndikucenjezani nazo, monga ndacita, kuti iwo akucita cita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.”
 
 
Ntchito za thupi ndi zoonekeratu 

Ntchito za thupi ndi zoonekeratu. Ntchito yoyamba ya thupi ndi “dama,” kutanthauza kuti kukhala mu ubwenzi osayenera ndi munthu osiyana ziwalo. Yachiwiri ndi “chiwewere.” Yachitatu ndi “codetsa.” Yachinai ndi “kukhumba zonyansa,” zomwe zikutanthauza kukhala ndi zilakolako. Ya chisanu ndi “kupembedza mafano,” imene ikutanthauza kutumikira mafano m’malo mwa Mulungu. Ya chisanu ndi chimodzi ndi “nyanga.” Yachisanu ndi chiwiri ndi “madano” Ngati munthu opanda Mzimu Woyera amayenda mogwirizana ndi thupi, sangakwanitse koma kuonetsa udani wake kwa ena mogwirizana ndi chibadwidwe chake chauchimo. Yachisanu ndi chitatu ndi “ndeu.” Ichi chikutanthauza kukangana ndi anzathu kapena achibale. Zina ndi “kaduka, zopsa mtima ndiponso zotetana.” Zonsezi ndi makhalidwe a anthu amene amayenda mwa thupi. 
Yakhumi ndi “magawano.” Ngati munthu akuyenda mogwirizana ndi thupi lokha, ndi kosatheka kwa iye kuchita ntchito ya mpingo ndipo pothera pake adzasiya mpingo mwakufuna kwake. Yakhumi ndi chimodzi ndi “mpatuko.” Iye amene akuyenda mwa thupi amachita chonchi kuti akhutiritse chifuniro chake. Koma moyo wotero ndi osiyana kwambiri ndi chifuniro cha Mulungu moti mapeto ake amathawa uthenga wabwino okoma. Mpatuko ukutanthauza kuchoka ku choonadi cha m’Baibulo. Palibe amene ali ndi chikhulupiliro m’mau a Mulungu ndi kuyenda mu Mzimu amachoka ku kuchifuniro cha Mulungu. “njiru, kuledzera, mcezo, ndi zina zotere;” nazonso ndi ntchito za thupi. Iwo amene amayenda mogwirizana ndi thupi lokha amachita zinthu zotere pamapeto pake. Ndi chifukwa chake Ambuye amati, “yendani mu Mzimu.” Ife, amene ndife wobadwa mwatsopano, tiyenera kuyenda mu Mzimu. 
Iwo amene ndi sanabadwe mwatsopano alibe chirichonse koma zilakolako za thupi m’mitima yawo. Ndi chifukwa chake amafuna kupezeka mu “chiwerewere, chodetsa, chonyansa, komanso mafano.” Atumiki abodza amene sanabadwe mwatsopano amachita za “nyanga” pa otsatira awo kuti awanyenge iwo kuti apereke ndalama zambiri. Amapereka ntchito zofunikira ndi maudindo akuluakulu a mpingo kwa iwo amene amapereka kwambiri. Iwo amene amakhala mwa thupi amaonetsa “madano” awo kwa ena. Amagawa mipingo kukhala zipembedzo zambiri, kuzitukumula ndi chipembedzo chawo ndi kudzudzula ena monga ampatuko. “ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko komanso njiru” Zonsezi zili mu mitima ya iwo amene sanabadwe mwatsopano. Chidzakhala chimodzimodzi ndi ife oyera mtima ngati tidzayenda mogwirizana ndi thupi. 
 
 
Mzimu umapangitsa Akristu obadwa mwatsopano kubala chipatso cha Mzimu Woyera 

Iwo amene abadwa mwatsopano ayenera kukhala akulalikira uthenga wabwino okoma. Monga kuli kovuta kwa ife kutsatira tokha Ambuye, tiyenera kuchita ntchito ya kutumikira uthenga wabwino okoma mwa kulumikizana ndi mpingo wa Mulungu. Tiyenera kupemphera pamodzi ndi kupereka mphamvu zathu kuti tikhale munthu amene amayenda mu uthenga wabwino okoma wa Mzimu. Anthu amene amayenda mu Mzimu amakhala polalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. M’mawu ena, kuyenda mogwirizana ndi thupi kukutanthauza kukhala ndi moyo wa iwe wekha pamene kuyenda mu Mzimu kukutanthauza kugwira ntchito yopulumutsa miyoyo ina. Akristu obadwa mwatsopano ambiri amakhala ndi moyo umenewu okoma. Amakhala chifukwa zabwino za ena. 
Kuli anthu ambiri kuzungulira dziko lonse lapansi amene sanamverepo ngakhale uthenga wabwino okoma. Timakonda anthu a ku Africa ndi ku Asia. Timakonda aliyense wa ku Europe ndi ku America komanso mu zilumba zapazokha. Tiyenera kuonetsa chikondi chathu powadziwitsa iwo uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. 
Tiyenera kuyenda mu Mzimu. Palibe lamulo pa chimenechi. “Koma cipatso ca Mzimu ndico cikondi, cimwemwe, mtendere, kuleza mtima, cifundo, kukoma mtima, cikhulupiriro, cifatso, ciletso; pokana zimenezi palibe lamulo” (Agalatiya 5:22-23). Kodi pali lamulo lina limene lingatsutsane ndi ili? Ai. Ili ndi lamulo la Mzimu limene tiyenera kumvera. Paulo anatiuza ife kuti tiyende mu Mzimu. Monga Ambuye wathu anaperekera moyo Wake kwa ife ochimwa, tiyenera kulalikira uthenga wabwino kwa ena. Kupulumutsa ena ku machimo awo ndiye kuyenda mu Mzimu. Tiyenera kuyenda mu Mzimu. 
Paulo anati mu Agalatiya 5:24-26, “Koma iwo a Kristu Yesu adapacika thupi, ndi zokhumba zace, ndi zilakolako zace. Ngati tiri ndi moyo ndi Mzimu, ndi Mzimunso tiyende. Tisakhale odzikuza, outsana, akucitirana njiru.” Tiyenera kukhalira kupulumutsa miyoyo yosochera ngati tikufuna kukhala mu Mzimu. Tiyenera kugwira ntchito ya Mzimu ndi kuyenda pamodzi Naye. Mzimu Woyera umene Mulungu anatipatsa umatitsogolera kuti tikhale ndi Yesu Kristu mu mitima yathu. Mzimu Woyera ndi mfumu ya chikondi. Mulungu amatigwiritsa ntchito ngati magalimoto a chikondi Chake. 
Paulo anati, “Koma iwo a Kristu Yesu adapacika thupi, ndi zokhumba zace, ndi zilakolako zace.” (Agalatiya 5:24). Iye ananenanso kuti iwo amene anabadwa mwatsopano anafa limodzi ndi Yesu Kristu. Iwo amene ndi obadwadi mwatsopano anafa kale limodzi ndi Yesu. Sitimazindikira zimenezi, koma tinafa ndi Yesu Kristu pamene anapachikidwa kuti alipire machimo athu. M’mawu ena, choona chakuti Yesu Kristu anapachikidwa chikutanthauza kuti inu ndi ine tinafa limodzi ndi Iye pa Mtanda. Imfa Yake inali imfa yathu ndipo kuuka Kwake kukusonyeza chitsimikizo cha kuuka kwathu. Inu ndi ine timakhala ndi kufa mwa Yesu Kristu kudzera mu chikhulupiliro chathu. Tiyenera kukhala ndi chikhulupiliro. Chikhulupiliro chathu chimatitsogolera ife kuti tiyende mu Mzimu. 
Mulungu anatipatsa ife mphamvu ya kuyenda mu Mzimu. Choncho, ife amene tinakhululukidwa ku machimo athu onse tiyenera kuyenda mu Mzimu. Iwo amene analandira Mzimu Woyera ayenera kukhala oyamikira kuti machimo awo anakhululukidwa ndi kuzipereka okha kulalikira uthenga wabwino okoma ku chipulumutso cha otayika. Ngakhale kuti munthu wakhululukidwa ku machimo ake ndipo ndi kubadwa mwatsopano, adzapatulidwa ku mpingo wa Ambuye ndipo sadzatha kumutumikira ngati adzakhala mogwirizana ndi zilakolako za thupi. Inu ndi Ine tiyenera kukhala mwa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu kufikira Tsiku la Ambuye wathu Yesu Kristu. 
 
 
Musakhale odzikuza koma khalani mwa kudzadzidwa kwa Mzimu Woyera 

Paulo anati, “Tisakhale odzikuza, outsana, akucitirana njiru.” Kodi kudzikuza ndi chiani? Ndi kuyenda mogwirizana ndi zilakolako za thupi. Pali anthu ambiri m’dziko lino amene amakhala mwa kudzikuza kwao. Anthu ambiri amasonkhanitsa ndalama, kulimbana ndi ukulu, kukonda kukoma kwa dziko ndi kukhalalira zampompano komanso zalero. Palibe kukhulupirika mu zimenezi, ndipo iwo adzaola ndi kusowa pamene nthawi ikupita. Ndi chifukwa chake anthu amene amayenda mogwirizana ndi thupi amatchedwa kuti odzikudza. Ngakhale kuti anthu ali ndi chuma, kodi muli mtendere weniweni ndiponso kukwaniritsidwa mu mitima yawo? Chipatso cha thupi pothera pake chimaola. Zinthu za dziko lapansi zilibe nchito ku miyoyo ya ena ndipo ndi za iwe wekha. Ndizabwino ku thupi la iwe wekha. 
Baibulo linena kuti, “Alipo wogawira, nangolemerabe; Aliponso womana comwe ayenera kupatsa nangosauka.” (Miyambo 11:24). Iwo amene sanabadwe mwatsopano amayesa kusunga ndalama kwambiri. Chifukwa zinthu zadziko lapansi e ndi chiri chonse kwa iwo, alibe chipinda mkati mwawo chosamalira ena. Ndi chifukwa chake amangofuna ndi kusamalira miyoyo yawo yokha. Koma m’Baibulo chinanenedwa kuti aliponso womana chomwe ayenera kupatsa nangosauka. Anthu amayenda mogwirizana ndi zilakolako za thupi, koma zotsatira zake ndi chimodzimodzi ndi zochokera kwa mbala ndipo mapeto ake ndi kufa. Zinthu zonsezi ndi chifukwa cha kudzikudza
 
 
Iwo amene amakonda kutsatira zokhumba za Mzimu 
 
Paulo ankafuna kukhala m’moyo wauzimu. Ndipo anachita zimenezo. Iye anatiphunzitsa ife kuti tikhale bwino kudzera mu mawu a Mulungu. Iye anati mu agalatiya 6:6-10, “Komai iye amene aphunzira mau, ayenera kucereza wophunzitsayo m’zonse zabwino. Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti cimene munthu acifesa, cimenenso adzacituta. Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, cocokera m’thupi adzatuta cibvundi; koma wakufesera kwa Mzimu, cocokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha. Koma tisaleme pakucita zabwino; pakuti pa nyengo yace tidzatuta tikapanda kufoka. Cifukwa cace, monga tiri nayo nyengo, ticitire onse cokoma, koma makamaka iwo a pa banja la cikhulupiriro.” 
Paulo anachenjeza iwo amene akudziwa mawu a Mulungu kuti agawane zinthu zonse zabwino ndi aphunzitsi awo. Chimene anatanthauza m’mawu akuti “m’zonse zabwino” chinali kusangalatsa Ambuye populumutsa miyoyo yosochera kudzera mu moyo oyenda mu Mzimu ndi kulalikira uthenga wabwino. Iwo amene ndi obadwa mwatsopano ayenera kulumikizana ndi iwo amene amaphunzitsa ndi kuyenda mu Mzimu ali ndi maganizo amodzi, chikondi ndiponso chiweruzo chofanana. 
“Ayenera kucereza wophunzitsayo m’zonse zabwino.” “m’zonse zabwino” kutanthauza kupulumutsa ena ku machimo awo kudzera mu mpingo. Paulo anatiuza kuti tichite zonse m’maganizo amodzi, m’pemphero limodzi ndiponso mukuzipereka kofanana. Tiyenera kuchita ntchito ya Ambuye pamodzi. 
Paulo anati, “Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti cimene munthu acifesa, cimenenso adzacituta.” Apa, “kunyoza” kukutanthauza “kutsutsidwa ndiponso kunyogodola.” Choncho “Musanyengedwe, Mulungu sanyozeka” kutanthauza kuti tisasutse kapena kunyogodola kwa Mulungu. Mwachitsanzo, munthu sayenera kutenga mau a Mulungu mopepuka, kuwamasulira m’mau a iye yekha ndi kulephera kukhulupilira mwa iwo. Paulo anati, “Pakuti cimene munthu acifesa, cimenenso adzacituta.” Ichi chikutanthauza kuti iye amene amafesa thupi adzakolola chibvundi, koma iye amene amafesa Mzimu dzakolola moyo wosatha. 
Kodi ndi chiani chomwe tidzatuta ngati tidzakhala mwa uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu? Tizalandira moyo wosatha ndi chipulumutso cha machimo athu. Tidzatuta zipatso za Mzimu potsogolera miyoyo ya ena ku chiombolo cha machimo awo ndi moyo wosatha kudzera mu madalitso a Mulungu. 
Koma kodi bwanji za anthu amene akukhalira thupi lawo? Amatuta chinyengo ndipo kulibe china chirichonse koma imfa pamapeto pake. Palibe china chotsala cha iwo pambuyo pa imfa yawo. Munthu amabadwa ndi manja opanda kanthu ndipo amafa ndi manja opanda kanthu. 
Ngati akuchita ntchito yopulumutsa ena ku machimo awo, adzakolola chipatso cha Mzimu ndi kukhala ndi moyo wosatha. Koma ngati akupitiriza kuyenda mogwirizana ndi zilakolako za thupi, amathera kukolola chibvundi. Ndiyeno adzakolola matemberero ndikupereka matemberero kwa ena. Choncho, Paulo, amene ankadziwa zonse za kukhala m’chikhulupiliro, anatichenjeza ife kuti tisayende mogwirizana ndi thupi. 
“Koma tisaleme pakucita zabwino; pakuti pa nyengo yace tidzatuta tikapanda kufoka.” Paulo anali mtumiki wa Mulungu amene anayenda mu Mzimu. Pamene anthu anaona m’Baibulo kuti anali kuyenda mu Mzimu, ena angaganize kuti Mzimu Woyera unamulamula kuti achite zinthu monga, “Paulo, kupita kumanzere ndi kukumana ndi wina” kapena “Uyenera kupewa munthu.” Koma ichi sichoona. 
Anayenda mu Mzimu polalikira uthenga wabwino wa chipulumutso kwa ena ndi kuthandiza kupulumutsa miyoyo yao. Paulo anatumikiranso Ambuye mwa kulumikizana ndi iwo amene anayendanso mu Mzimu. Mwa Akristu, panali anthu amene sankafuna kuyenda mu Mzimu koma kuyenda mogwirizana ndi zilakolako za thupi. Iwo sanamulandire Paulo koma kutsutsana naye ndiponso ngakhale kumunyoza. Paulo ananena kuti sankafuna china chirichonse kuchitika ndi iwo amene anamuukira ndi kunyoza ophunzira a Yesu Kristu. 
Ngati mukufuna kuyenda mu Mzimu, muyenera kukhala mwa uthenga wabwino. Amdulidwe ananzunza Paulo. Mu agalatiya 5:11 akunena kuti, “Koma ine, abale, ngati ndilalikiranso mdulidwe, ndizunzikanso bwanji? Pamenepo cikhumudwitso ca mtanda cidatha.” Amdulidwe anali iwo amene akudziwa kuchita za mdulidwe, kunena kuti, “Ngakhale kuti munthu wabadwa mwatsopano pokhulupilira mwa Yesu, ayenera kudulidwa. Ngati sanadulidwe ku thupi lakhungu lakusonga, ndiye kuti simwana wa Mulungu.” Kodi ndi chifukwa chiani anamunzunza iye? Paulo anakhulupilira kuti chiombolo ndi madalitso a moyo osatha zimabwera kudzera kokha mu chikhulupiliro cha mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda. Ichi ndi chimene ankalalikira. 
Chikhulupiliro chimene chimapangitsa anthu kukhala olungama chichokera mu kuphunzira choonadi ndi kuchilalikira icho. Paulo anaona choonadi cha madzi ndi Mzimu kukhala chofunika kwambiri. Anakhulupilira kuti iwo amene anadziwa choonadi angayende mu Mzimu ndipo kuti palibe chifukwa chodulidwa. Ichi ndi chimene analalikira. Koma amdulidwe anakhulupilira kuti mdulidwe unali mbali yaikulu pa chikhulupiliro cha munthu mu chipulumutso. Komabe, palibe uthenga wina wabwino oposa umene Mulungu anaugwetsa ndipo motero sitiyenera kuikapo kapena kuchotsapo chilichonse kuchimenecho. 
Pamene Paulo ankayenda mu Mzimu, iye anakanidwa ndi kunzunzidwa ndi Ayuda amnzake. “Onse amene afuna kuonekera okoma m’thupi, iwowo akukangamizani inu mudulidwe; cokhaco, cakuti angazunzike cifukwa ca mtanda wa Kristu. Pakuti angakhale iwo omwe odulidwa sasunga lamulo; komatu afuna inu mudulidwe, kuti akadzitamandire m’thupi lanu. Koma kudzitamandira ine konse konse, iai, koma mu mtanda wa Ambuye wathu Yesu Kristu, amene mwa Iye dziko lapansi lapacikidwira ine, ndi ine ndapacikidwira dziko lapansi. Pakuti mdulidwe ulibe kanthu, kusadulidwa kulibe kanthunso, komatu wolengedwa watsopano.” (Agalatiya 6:12-15). Ndipo Paulo anati kwa amdulidwe, “Onse amene afuna kuonekera okoma m’thupi, iwowo akukangamizani inu mudulidwe; cokhaco, cakuti angazunzike cifukwa ca mtanda wa Kristu.”
Paulo anadzudzula iwo amene anali kuyenda mogwirizana ndi zilakolako za thupi. Anali kuyendadi mogwirizana ndi zilakolako za thupi ndipo kunali anthu ambiri monga iwo. Koma Paulo anathetsa mgwirizano pakati pao. Paul anati, “Koma kudzitamandira ine konse konse, iai, koma mu mtanda wa Ambuye wathu Yesu Kristu.” Yesu Kristu anabatizidwa ndi Yohane kuti achotse machimo onse a dziko ndipo anafa pa Mtanda kuti apulumutse Paulo ndi anthu onse ambiri monga Ambuye wathu Mulungu awaitanira. Paulo anati, “Koma mu mtanda wa Ambuye wathu Yesu Kristu, amene mwa Iye dziko lapansi lapacikidwira ine, ndi ine ndapacikidwira dziko lapansi. Pakuti mdulidwe ulibe kanthu, kusadulidwa kulibe kanthunso, komatu wolengedwa watsopano.” Paulo, amene anali wakufa kudziko, anakhalanso kudzera mwaYesu Kristu. 
Ndife akufa mwa Yesu Kristu. Koma nthawi zina timaiwala choonadi chimenechi. Tiyenera kukhulupilira icho. Ngati tiribe chikhulupiliro mu choonadi chimenechi, ndife omangidwa ndi zilakolako za thupi ndi mabanja athu, ndipo chimenechi chimaletsa kuti tiyende ndi Ambuye. Thupi lathu ndi lofoka kwambiri kotero kuti ngakhale mabanja athu sangatithandize kuti titsatire Iye. Ndi Ambuye yekha amene angatithandize ife. Koma tsopano tapachikidwa ku dziko lapansi. Kodi munthu wakufa angathandize bwanji anthu a dziko lapansi mu zochitika za dziko lapansi? Anthu amene ndi akufa m’dziko lino sangakhale ndi zinthu za dziko. 
Yesu anaukitsidwa. Kuukitsidwa Kwake kunatilola ife kuti tibadwe mwatsopano kukhala moyo wauzimu. Pano tili ndi ntchito yatsopano, banja latsopano, chiyembekezo chatsopano. Ndife anthu obadwa mwatsopano. Ife, monga asilikali a kumwamba, tili ndi udindo wakulalikira mawu a Mulungu. Paulo anaulula kuti anakhala munthu pothandiza ena kupeza chipulumutso osati kudzera mu zinthu zakuthupi koma kugwiritsa ntchito njira zauzimu. Iye anati anali atafa kale ndipo anabadwa mwatsopano kudzera mwa Yesu Kristu. Tiyeni tiyeseyese kukhala anthu amene tiyesa kupereka chibvomerezo chofanana ku zikhulupiliro zathu. 
Paulo anati mu Agalatiya 6:17-18, “Kuyambira tsopano kulibe munthu andibvute, pakuti ndiri nayo ine m’thupi mwanga mikwingwirima ya Yesu. Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu cikhale ndi mzimu wanu, abale. Amen.” Paulo anasenza zipsera za Ambuye Yesu. Sanasamalire za thanzi lake kwa Ambuye kuti ayende mu Mzimu. Iye sanathenso ngakhale kulemba, popeza pang’ono pang’ono anasiya kuona. Choncho makalata ambiri a Paulo analembedwa ndi katswiri monga Tertius pamene iye anali kunena Mau a Mulungu. Ngakhale kuti anali ofoka kuthupi, anali okondwa kuyenda mu Mzimu ndipo anati, “Cifukwa cace sitifoka; koma ungakhale umunthu wathu wakunja ubvunda, wa m’kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku” (2 Akorinto 4:16). 
Paulo anachenjeza ife kuti tikhale anthu amene timayenda mu Mzimu. Ananenanso kuti, “Kuyenda mu Mzimu kukutanthauza kukhala chifukwa cha uthenga wabwino.” Inu ndi ine tiyenera kusunga m’maganizo kuti kodi kuyenda mu Mzimu chikutanthauzanji. Sitiyenera kutsata zinthu zachabe ndipo m’malomwake titumikire ndi kukhala mu uthenga wabwino. Tiyeni tiyende mu Mzimu mwa chikhulupiliro m’miyoyo yathu yonse. 
Tsopano mwa kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, Mzimu weniweni uli mu mitima yathu. Mulungu mosangalala adzayankha ngati tidzapemphera mogwirizana ndi uthenga wabwino. Kubala chipatso cha Mzimu kukutanthauza kuyenda mu Mzimu ndi kuombola miyoyo. Mungabale chipatso cha Mzimu, chotchedwa chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, komanso chiletso, ngati mungayende mu Mzimu ndi kukhala mwa uthenga wabwino. Kuti tilalikire uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, tiyenera kuzunzidwa, kukhalabe opilira, kuchita kukoma mtima ndi kuchita zabwino kwa osochera. 
Zipatso za Mzimu zimaberekedwa mwa iwo amene amapulumutsa miyoyo yosochera pochita zabwino ndi kulalikira uthenga wabwino umene umapangitsa kuti alandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Ichi ndi chimene chimachitika kuti tibale zipatso za Mzimu ndi kuyenda mu Mzimu.