(Aefeso 5:6-18)“Asakunyengeni inu munthu ndi mau opanda pace, pakuti cifukwa ca izi umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera. Cifukwa cace musakhale olandirana nao; pakuti kale munali mdima, koma tsopano muli kuunika mwa Ambuye; yendani monga ana a kuunika, pakuti cipatso ca kuunika ticipeza m’ubwino wonse, ndi cilungamo, ndi coonadi, kuyesera cokwenderetsa Ambuye nciani; ndipo musayanjane nazo nchito za mdima zosabala kanthu, koma maka-makanso muzitsutse; pakuti zocitidwa nao m’tseri, kungakhale kuzinena kocititsa manyazi. Koma zinthu zonse potsutsika ndi kuunika, zionekera; pakuti conse cakuonetsa ciri kuunika. Mwa ici anena, Khala maso wogona iwe, nuuke kwa akufa, ndipo Kristu adzawala pa iwe. Potero, penyani ubwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akucita macawi, popeza masiku ali woipa. Cifukwa cace musakhale opusa, koma dziwitsani cifuniro ca Ambuye nciani. Ndipo musaledzere naye vinyo, m’mene muli citayiko; komatu mudzale naye Mzimu.”
Kodi tiyenera kuchita chiani kuti tisunge miyoyo yathu yodzala ndi Mzimu Woyera?
Tiyenera kuzikana tokha, kunyamula mtanda, ndi kukana maganizo athu oipa, kuzipereka tokha kulalikira uthenga wabwino.
Kuti “tikhalebe ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera,” tiyenera kudzipereka tokha kulalikira uthenga wabwino. Kuti tikhale ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera, choyamba tiyenera kulandira dalitso limene limapangitsa kuti Mzimu Woyera ukhale m’mitima yathu. Kuti tilandire kulowedwa kwa Mzimu Woyera tiyenera kukhala ndi mtundu uwu wa chikhulupiliro, ndiye kuti, tiyenera kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu umene Mulungu anatipatsa ife. Pokhala ndi chikhulupiliro chimenechi, tizalandira dalitso limene limapangitsa kuti Mzimu Woyera ukhale mwa ife.
Kodi iwo amene ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera akufuna moyo odzala ndi Mzimu Woyera? Indedi amafuna. Koma kodi ndi chifukwa chiyani ena a iwo sangakhale ndi moyo umenewu? Chifukwa ndi chakuti mavuto awo amapita patsogolo kupyola ntchito ya Mulungu, kutanthauza kuti sangayende ndi Iye. Kuti tikhalebe ndi moyo odzadza ndi Mzimu Woyera, tiyenera kuphunzira ndi kukhulupilira mu ntchito ya Mulungu. Choyamba pa zonse, tiyeni tione mu Baibulo kuti tipeze kuti moyo wotani ndiponso chikhulupiliro chimene tiyenera kukhala nacho.
Kodi n’chifukwa chiani anthu ena sangathe kukhala ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera?
Choyamba, tinganene kuti ndi chifukwa chakuti sangadzikane okha. Baibulo linanena kuti okhawo amene amadzikana okha ndi amene angayende ndi Ambuye. Pakuti kupeza moyo odzala ndi Mzimu Woyera ndi kosatheka kudzera mu mphamvu ya munthu, aliyense ayenera kukhala ndi chikhulupiliro cha kukhazikika kwa Mzimu Woyera, kotero kuti azisiye yekha. Ngakhale kwa iwo amene ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera, ndi kovuta kwa iwo kudzikana okha kopanda kukhala okhudzidwa ndi Ufumu wa Mulungu. Motero, kuti tikhale ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera, tiyenera kutumikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Pokhapo ndi pamene munthu angadzikane yekha ndi kukhala mtumiki wachilungamo.
Mu Mateyu 16:24-26 anena kuti, “Pomwepo Yesu anati kwa ophunzira ace, Ngati munthu afuna kudza pa mbuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wace nanditsate Ine. Pakuti iye amene afuna kupulumutsa moyo wace adzautaya: koma iye amene ataya moyo wace cifukwa ca Ine, adzaupeza. Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wace? Kapena munthu adzaperekanji cosintha ndi moyo wace?”
Chifukwa chimene anthu ena amene ndi obadwa mwatsopano sangakhale ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera ndi chakuti amalephera kukana zilakolako za thupi lao. Ngakhale anthu amene ali ndi kukhazikika kwa Mzimu angatsatire Mzimu Woyera pokhapo ngati asiya zilakolako za thupi lao. Pali mbali zambiri za moyo wa thupi zimene tiyenera kusiya kuti titsatire Ambuye. Ambuye anati, “Adzikane yekha, natenge mtanda wace nanditsate Ine.”
Pakuti chisamaliro cha thupi chiri imfa; koma chisamaliro cha Mzimu chiri moyo ndi mtendere. Anthu amene amafuna kuyenda mu Mzimu ayenera kusiya moyo wa thupi. Okhawo amene amayesa kupereka nsembe ndi amene angakhalebe ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera. Ichi ndi choonadi cha kudzadzidwa kwa Mzimu Woyera.
Kodi ndi chiti chimene mukufuna kutsatira, Ambuye kapena dziko? Mogwirizana ndi chosankha chanu, moyo odzala ndi Mzimu Woyera kapena moyo wa zilakolako ndi wanu. Ngati mukufunadi kukhala moyo odzala ndi Mzimu Woyera, chisankho ndi chanu. Mulungu anatipulumutsa ku machimo athu onse ndi kutipatsa mphatso ya kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Koma ndikufuna kwanu kusankha kaya kukhala moyo odzala ndi Mzimu Woyera. M’mawu ena, moyo odzala ndi Mzimu Woyera si okonzedweratu kapena chifuniro cha Mulungu. Moyo odzala ndi Mzimu Woyera umadalira kokha pa zofuna za iwo a ife amene timakhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu.
Muyenera kukhala ndi chifuniro chokhala ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera
Ngati muli ndi chifuniro cha kukhala ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera, Mulungu adzachilola. Iye adzathandiza ndi kukudalitsani. Koma ngati simukufuna, muyenera kusiya moyo odzala ndi Mzimu Woyera.
Mungalandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera pongokhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndipo osati mwa chifuniro chanu. Koma kukhala ndi kusunga moyo odzala ndi Mzimu Woyera zikudalira kwathunthu pa chifuniro chanu.
Motero, ngati mukufuna moyo odzala ndi Mzimu Woyera, muyenera kuyeza chifuniro chanu ndi kupempha thandizo la Mulungu. Ngati tikufunadi miyoyo yodzala ndi Mzimu Woyera, Mulungu adzatidalitsa ndipo adzakwaniritsa zokhumba zathu. Koma kuti tikwanitse cholinga chathu, tiyenera kukana zilakolako zathupi.
Chachiwiri, kuti tikhale ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera, tiyenera kunyamula mitanda yathu. Tiyenera kukhala ndi kuyenda mwa chifuniro cha Mulungu ngakhale mu m’nyengo zovuta. Ichi ndi chimene chikutanthauza kukhala ndi moyo wachilungamo odzala ndi Mzimu Woyera.
Ndipo chachitatu, Ambuye anati, “Pakuti iye amene afuna kupulumutsa moyo wace adzautaya: koma iye amene ataya moyo wace cifukwa ca Ine, adzaupeza. Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wace? Kapena munthu adzaperekanji cosintha ndi moyo wace?” Ichi chikutanthauza kuti kutsatira Ambuye ndi kofunika ku miyoyo yathu. Indedi, ngati tingamutsatire Iye, mzimu komanso thupi lathu zidzachita bwino koma ngati sitidzatsatira Iye ndi kusankha kukhala ndi miyoyo ya ife tokha, mzimu ndi thupi lathu zidzaonongedwa.
Kodi n’chifukwa chiyani sitingakhale ndi miyoyo yodzala ndi Mzimu Woyera? Chifukwa ndi chakuti sitimakana maganizo athu, zotchedwa zilakolako za thupi. Pamene tikutsatira Yesu, Mzimu umalimbitsa mkati mwathu ndipo motero angatitsogolere ife ndi mphamvu zazikulu.
Mu Aefeso 5:11-13 munena kuti “Ndipo musayanjane nazo nchito za mdima zosabala kanthu, koma maka-makanso muzitsutse; pakuti zocitidwa nao m’tseri, kungakhale kuzinena kocititsa manyazi. Koma zinthu zonse potsutsika ndi kuunika, zionekera.” Akristu sayenera kugwirizana ndi ntchito zosabala zipatso za mdima. Koma ngati tidziika tokha mu ntchito za mdima zosabala chipatso, Mulungu akutiuza kuti tiziike poyera. Tiyenera kudzudzulidwa ndi ntchito zathu za mdima, popeza ndi zochititsa manyazi ngakhale kulankhula za zinthu zimenezo zimene zimachitidwa ndi iwo mu mdima. Koma zinthu zonse potsutsika ndi kuunika, zionekera.
Kodi ndani oyenera kuonetsa ndi kulankhula zinthu zochititsa manyazi zonsezi? Ngati ena, abale kapena alongo anu ndi akapolo a Mulungu sangathe kuzionetsa, muyenera kuzionetsa inu nokha. Kunanenedwa kuti zinthu zonse zomwe zaonekera zimatsutsikandi kuunika. Motero tiyenera kuvomereza zoipa zathu zimene timachita kuti sizabwino, ndi kutsogoleredwe ndi Mzimu Woyera kuti tionetse ntchito zosabala zipatso za mdima ife tokha kapena kudzera mwa mtsogoleri wathu.
M’dziko lino, zinthu zonse zimene zimaonetsedwa zimatha ngati zadzudzulidwa koma m’dziko la Mulungu, zinthu zonse zoonekera zimatutsidwa ndi kuunika, popeza chimene chimaonetsa ndi kuunika. Popeza tili kutali ndi ungwiro, timachita machimo ambiri mosadziwa m’dzikoli. Komabe, pamene tikaika kuunika kwa mawu a Mulungu pa ife tokha, timakhala ndi chikumbumtima cha machimo ena ndipo timatha kuwavomereza. Ndipo motero ndi chifukwa cha chimenecho kuti timayamikira Mulungu kosatha.
Chifukwa Yesu anachotsa machimo ndi mphulupulu zathu zonse, ndipo chilungamo chonse cha Mulungu chinakwaniritsidwa pamene anabatizidwa mu Mtsinje wa Yordano, tikutha kuonetsedwa ndi kuunika kudzera mu chilungamo cha Mulungu. Machimo mabiliyoni ambiri amene munthu anachita anaperekedwa kwa Yesu pamene Yohane anabatiza Iye. Iye ndi Mwanawankhosa wa Mulungu amene anachotsa machimo a dziko, kufa pa Mtanda kuti aweruzidwe chifukwa cha iwo, ndipo anaukitsidwa. Yesu anakhululuka machimo onse a munthu ndipo pamene ananena kuti, “kwatha” (Yohane 19:30), mtundu onse wa anthu unapulumutsidwa. Timakhala oyeretsedwa kudzera mu chikhulupiliro chathu mu zimene Yesu Kristu anachita. Popeza machimo athu anakhululukidwa, tingabwerenso mu kuunika ndi kutsatira Mulungu mwa chilungamo.
Mulungu anatiuza ife kuti tichite machawi
Paulo ananena kuti ngati tikufuna kukhala odzala ndi Mzimu Woyera, tiyenera kuchita machawi. Mu Aefeso 5:16-17 munena kuti “Akucita macawi, popeza masiku ali woipa. Cifukwa cace musakhale opusa, koma dziwitsani cifuniro ca Ambuye nciani.” Ngati tikufuna kukhala ndi umoyo odzala ndi Mzimu Woyera, tiyenera kuchita machawi ndipo tisakhale opusa. Tiyenera kumvetsa kuti chifuniro cha Ambuye ndi chiani ndi kuchita icho. Tiyenera kusankha chimene chili choyenera: moyo okhulupirika ku thupi lathu kapena uja ozipereka kwa Mulungu.
Pamene tabadwa mwatsopano, Mzimu Woyera umakhala mwa ife. Ngati talandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera, chikutanthauza kuti Mbuye wathu ndi Yehova ndipo Iye ndi Mfumu yathu. Iye Yekha ndiye Mpulumutsi wathu ndipo tiyenera kuvomereza Iye kwathunthu kuti ndi Mulungu wathu. Iye ndi Mbuye wathu yekha. Iye ndi Mbuye amene anapanga ine, anandikhululukira machimo anga onse ndi kundidalitsa. Ndipo Iye ndi Mfumu amene ali ndi mphamvu pa moyo wanga ndi imfa, madalitso ndi matembelero. Tiyenera kuvomereza kuti Ambuye ndi Mbuye Iye yekha ndiponso Mulungu, choncho tiyenera kumumvera Iye mu miyoyo yathu yonse.
Tiyeni tione chimene chinanenedwa pa Afilipi 2:5-11. “Mukhale nao mtima m’kati mwanu umene unalinso mwa Kristu Yesu, ameneyo, pokhala nao maonekedwe a Mulungu, sanaciyesa colanda kukhala wofana ndi Mulungu, koma anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe a kapolo, nakhala m’mafanizidwe a anthu; ndipo popezedwa m’maonekedwe ngati munthu, anadzicepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda. Mwa icinso Mulungu anamkwezetsa Iye, nampatsa dzina limene liposa maina onse, kuti m’dzina la Yesu bondo liri lonse lipinde, la za m’mwamba ndi za padziko, ndi za pansi pa dziko, ndi malilime onse abvomere kuti Yesu Kristu ali Ambuye, kucitira ulemu Mulungu Atate.”
Paulo anati, “Mukhale nao mtima mkati mwanu.” Ananena kuti uwu unali Mtima wa Yesu Kristu. Chimene Paulo ananena chinali chakuti “mtima” ndi wa Yesu, amene anali Mulungu Mlengi ndipo anabwera padzikoli kudzapulumutsa anthu Ake ku machimo awo mogwirizana ndi chifuniro cha Atate Ake. Ambuye anabwera padziko lino ndi kuchotsa machimo onse a dziko kudzera mu ubatizo Wake ndi Yohane. Ndipo pamene anafa pa Mtanda machimo a dziko anathetsedwa ndi Iye. Iye ndiyeno anaukitsidwa pa tsiku lachitatu ndi kukhala Mpulumutsi wathu.
Chifukwa chimene Yesu Kristu, Mlengi, anabwerera padziko lino chinali kudzapulumutsa ife. Anaonetsa chikondi Chake kwa ife kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi wa pa Mtanda. Zolengedwa zonse ziyenera kugwadira Iye ndi kuthokoza chikondi Chake chimene chinatipatsa chikhululukiro cha uchimo mwa kudzichepetsa Iye yekha ngati cholengedwa ngakhale kuti Iye ndi Mlengi. Ndi chifukwa chake zolengedwa zonse ziyenera kubvomereza kuti Iye ndiye Mpulumutsi wawo oona. Iye anatipangitsa kuti tibvomereze kuti Iye si Ambuye wa zolengedwa zokha komanso ndi Ambuye wa chilungamo chonse kwa ife.
Ife, amene timakhulupilira mwa Mulungu ndipo tili ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera, tiyenera kukhulupilira kuti ‘Mulungu ndi Mbuye wathu weniweni kwa ine’ ndi kukhala ndi chikondi cha Yesu Kristu mu mtima mwathu. Tiyenera kukhala ndi chikhulupiliro chakuti mbuye wathu siife tokha koma Yesu Kristu, amene analenga ndi kutipulumutsa ife ku machimo athu onse. Ndipo tiyeneranso kukhala ndi chikhulupiliro chakuti Iye ndi Mbuye amene amatipanga ife kukhala ndi moyo odalitsika ndi kukonzekera zonse zathu ndi kutigwilira ntchito.
Kuli anthu ambiri amene safuna kusinthanitsa ambuye pamene badwa mwatsopano. Kuli ambiri amene ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera koma akukakamira kuti ndi ambuye pa iwo okha. Moyo odzala ndi Mzimu Woyera ndi moyo umene umatsatira Mulungu. Moyo otere sungapatidwe mu tsiku limodzi koma ndi zotheka pokhapo ngati timakhulupilira kuti Yesu ndi Mbuye wa miyoyo yathu ndipo M’modzi amene anatilenga ife ndi zolengedwa zina zonse m’dziko lapansi. Tiyenera kukhala ndi chikhulupiliro kuti titumikire Yesu Ambuye wathu, Mbuye ndiponso Mulungu, amene anatipulumutsa ife ku machimo athu ndi kutipatsa moyo osatha mu ufumu wa Kumwamba.
Tiyenera kubala choonadi m’mitima yathu. Anthu ambiri akukhala ndi miyoyo yawo ngati ambuye iwo okha. Amateteza ndi kusunga ulamuliro pa miyoyo yawo. Koma tsopano ndi nthawi yosintha ambuye. Tsopano takhala amene tikudziwa Mulungu, ndipo motero Ambuye wathu ofunika ndi Yehova.
Tonsefe tili ndi uchimo mu mitima yathu ndipo tiyenera kuweruzidwira ku gahena chifukwa cha zolakwa zathu. Koma tinapeza Mulungu kudzera mu chikhulupiriro chathu mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Mulungu amatikonda kwambiri kotero kuti anabwera padziko lapansi, kuchotsa machimo athu onse mwa kubatizidwa ndi Yohane ndi kufa pa Mtanda kuti akhale Mpulumutsi wathu weniweni. Ndipo kudzera mu chikhulupiliro chathu mwa Mulungu, tinaomboledwa ku machimo athu onse. M’mawu ena, tinalandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera.
Baibulo limanena kuti, “Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Kristu, siali wace wa Kristu” (Aroma 8:9). Pamene tinalandira chiombolo Chake, chimene ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera, tinakhala ana a Mulungu. Mzimu Woyera ndi Mulungu kwa ife ndipo tiyenera kuyenda mu chilungamo cha Mulungu pansi pa malangizo a Mzimu Woyera. Kuti tikhale motero, tiyenera kusiya ukatswiri wathu pa ife tokha. Pamene tinakumana ndi Yesu ndipo tinaomboledwa ndi Iye, tiyenera kupanga Iye kukhala wathu ndiponso Mbuye wathu Yekha.
Tiyenera kupereka mipando yachifumu m’mitima yathu kwa Yesu
Sitingatsatire Ambuye ngati timaziona tokha ngati ambuye wa miyoyo yathu. Pamene Mulungu watilamula kuti timtumikire, tizanena kuti “Inde” popanda kuchedwa ngati sindife ambuye pa ife tokha. Apo ayi, tinganene kuti “Kodi n’chifukwa chiyani ndiyenera kukuchitirani?” Munthu amene ndi mbuye payekha adzakana kuchita zimene Mulungu akufuna kuti iye achite, akuganiza kuti, “Ayenera kundipempha monga Mpulumutsi kuti ndimuchite zimene Iye akufuna.” Kwa munthu otere, malangizo a Mulungu ndi opanda kanthu koma achabe ndiponso mawu ovutitsana.
Komabe, kuti tidzadzidwe ndi Mzimu Woyera, tiyenera kumvera lamulo Lake. Sitingakhale ng’ombe zimene zikupita kukhaphedwa, koma m’malo mwake tiyenera kuzipereka kuti titsatire Mulungu. Tiyenera kutsatira Mulungu, Mpulumutsi wathu, amene amatitsogolera ku njira yachilungamo. Mulungu ndi Ambuye, amene anatidalitsa ife ndi chipulumutso. Ngati tikumutumikira monga Mbuye wathu ndi kusunga malamulo Ake, tingadzadzidwe ndi Mzimu Woyera. Ngati inu ndi mamembala a banja lanu mwapereka ufumu wanu kwa Yesu ndi kumuika kukhala pamwamba pa aliyense, muzakhala ndi chisomo ndiponso madalitso mu miyoyo yanu.
Mwina munaona chithunzithunzi cha munthu amene akuyendetsa bwato lake molimbana ndi mphepo ya mkuntho ndipo Yesu waimilira pambali pake. Pamene zikuoneka ngati tikukwanitsa zovuta za miyoyo yathu ndi kugwira ntchito ya Ambuye, ndi Ambuye wathu Yesu Kristu amene akutitsogolera ife ndi kutigwira manja. Ndi Mulungu Wamphamvu zonse amene amaona kutsogolo kwa miyoyo yathu. Iye anatipulumutsa. Amatiteteza kwa Satana, kutsitsogolera ndipo ali ndi mphamvu pa miyoyo yathu.
Popeza anakhala Mbuye wathu, Iye amatha kutiyang’anira ndi kutidalitsa. Koma ngati sitizindikira Iye ngati Mbuye wathu, sangagwire ntchito imeneyo. Popeza ndi Mulungu wa umunthu, samatikakamiza ife kuti timvere chifuniro Chake. Ngakhale kuti Iye ndi Mulungu Wamphamvu zonse, samachita chilichonse kwa ife ngati sitizipereka kuti titumikire Iye ngati Mbuye wathu ndi kupempha thandizo.
Tayirani zinthu zonse pa Iye
tayirani zinthu zonse pa Iye kotero kuti akwaniritse Umbuye Wake pa inu. Tumikirani Iye ndipo vomerezani kuti Iye ndiye Mbuye wathu. Popeza tili kutali ndi ungwiro, tiyenera kuponya zinthu zonse pa Iye ndi kupereka zonse zathu pa Iye. Pamene taponya mabanja athu, miyoyo yamasiku onse ndi zina zonse pa Iye, tizalandira nzeru kwa Mulungu ndi kukhala okwanitsa kukhala m’mene Iye akufunira, kukwanitsa mavuto onse ndi chikhulupiliro ndi mphamvu zimene Mulungu anapereka kwa ife.
Mavuto athu tsopano ndi omwe amakhala Mbuye wathu, kutanthauza kuti ngati tidzatsatira Yesu Mulungu yekha Wamphamvu zonse, Iye adzatisamalira. Tizatha kukhala ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera ndi kusangala ndi mtendere umene uli mwa Iye. Ngati Akristu achikhulupiliro, tiyenera kugwada pamaso pa Mulungu, kuvomereza ndi kumutumikira ngati Mbuye wathu.
Tiyeni tione zimene akunena mu Afilipi 3:3 za mtundu wa chikhulupiliro umene tiyenera kukhala nawo kuti tikhale ndi kuzadzidwa kwa Mzimu Woyera. “Pakuti ife ndife mdulidwe, wakutumikira popembedza ndi Mzimu wa Mulungu, nadzitamandira mwa Yesu Kristu, osakhulupirira m’thupi.” Chimene chikutanthauza akati ‘mdulidwe’ apa ndi iwo amene akulambira Mulungu mu Mzimu, kusangalala mwa Kristu Yesu, ndi kukhala opanda chilimbikitso chathupi.
Kukhala ngati odulidwa kukutanthauza kudula uchimo onse uli mu mtima mwathu ndi kupereka kwa Yesu Kristu, amene anabatizidwa ndi Yohane. Iwo amene akutsogoleredwa ndi Mzimu amakongoletsa miyoyo yawo kwa Mzimu. Amatumikira Mulungu ndi kusangalala mwa Kristu Yesu kunena kuti, “Yesu wanditsogolera kuti ndikhale ndi moyo waulemerero umenewu. Anandipanga kukhala olungama ndi kundidalitsa. anandipatsa chisomo chake chonse chimene ndinali kufuna kuti ndimutumikire.” Tiyenera kukhala motere. Uwu ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera. Paulo anati “Cifukwa cace mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale mucita kanthu kena, citani zonse ku ulemerero wa Mulungu” (1 Akorinto 10:31).
Mu Afilipi 3:13-14 akunena kuti, “Abale, ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kucigwira: koma cinthu cimodzi ndicicita; poiwaladi zam’mbuyo, ndi kutambalitsira zam’tsogolo, ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Kristu Yesu.” Mulungu anatiuza kuti tiiwale zinthu zimene zili kumbuyo kwathu kale ndi kufikira ku zinthu zimene zili kutsogolo. Tiyenera kulondola kutsatira cholinga chathu. Mosasamala kanthu za chilungamo chathu kapena zolakwa zathu, tiyenera kuiwala zinthu zimenezo zili kumbuyo kwathu ndi kuyesa kufika kutsogolo ku zinthu zili kutsogolo ndi kulondola ku cholinga chathu. Cholinga chimenechi ndi kutumikira chifuniro Chake kugwirizitsitsa Yesu Kristu pokhulupilira mwa Iye.
Tili kutali ndi ungwiro, choncho tilipafupi kugwa pansi pamene tikumva chiyeso cha thupi. Komabe, poyang’ana kwa Mulungu ndi kukhala ndi chikhulupiliro, tingataye kufoka kwathu konse ndi mphulupulu. Pamene Yesu Kristu anabatizidwa ndi Yohane ndi kufa pa Mtanda, machimo athu onse anaperekedwa kwa Iye. Pamene anakhala Mpulumutsi wathu kudzera mu kuukitsidwa, tinapatsidwa miyoyo yatsopano tikuyamikira chikhulupiliro chathu mwa Iye. Motero, tiyenera kutaya zinthu zonsezo zimene zili kumbuyo kwathu, kuthamangira ku zinthu zili kutsogolo ndi kuyandikira ku cholinga chathu
Kupitiriza ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera
Tiyenera kufika kutsogolo ku zinthu zimene zili patsogolo ndi kuyandikira ku cholinga chapamwamba. Ndili ndi chiyembekezo kuti mungaiwale zinthu zonse zakale mwamsanga ngati zikukulemetsani. Pali zinthu zambiri zimene sizingachitike chifukwa cha kufoka kwathu, koma izo ndi zopanda ntchito chifukwa chimene chili chofunikira chagona kutsogolo. Popeza tsogolo ndiye lofunikira kwambiri, tiyenera kupereka ufumu wathu kwa Yesu Kristu kudzera m’chikhulupiliro ndi kutsogoleredwa ndi Iye. Tiyenera kulola Iye kuti asankhe m’mene tizayenera kukhalira mtsogolo ndi kuchita zimene zili zokondweretsa Iye.
Tiyenera kukhala monga m’mene anakhalira ophunzira
Tingakhale ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera pokhapo ngati takhala olimba m’chikhulupiliro chathu mu chikhululukiro cha uchimo. Ichi ndi chofunikira kwambiri. Tiyeni tione pa 2 Timoteyo 2:1-10. “Ndipo iwe, mwana wanga, limbika m’cisomo ca m’Kristu Yesu. Ndipo zimene wazimva kwa ine mwa mboni zambiri, zimwezi uikize kwa anthu okhulupirika, amene adzadziwa kuphunzitsa enanso. Umve zowawa pamodzi nane monga msilikari wabwino wa Kristu Yesu. Msilikari sakondwa nazo nchito wamba, kuti akakondweretse iye amene adamlemba usilikari. Koma ngatinso wina ayesana nao m’makani a masewero, sambveka korona ngati sanayesana monga adapangana. Wam’munda wogwiritsitsa nchitoyo ayenera akhale woyamba kulandira zipatsozo. Lingirira cimene ndinena; pakuti Ambuye adzakupatsa cidziwitso m’nzonse. Kumbukila Yesu Kristu wouka kwa akufa, wocokera m’mbeu ya Davide, monga mwa Uthenga Wabwino wanga; m’menemo ndimva zowawa kufikira zomangira, monga wocita zoipa; koma mau a Mulungu samangika. Mwa ici ndipirira zonse, cifikwa ca osankhika, kuti iwonso akapeze cipulumutsoco ca mwa Kristu Yesu, pamodzi ndi ulemerero wosatha.”
Monga Paulo ananenera kwa Timoteyo, Mzimu Woyera umanena kwa ife kuti, “Limbika m’cisomo ca m’Kristu Yesu. Ndipo zimene wazimva kwa ine mwa mboni zambiri, zimwezi uikize kwa anthu okhulupirika, amene adzadziwa kuphunzitsa enanso.”
“Limbika m’cisomo ca m’Kristu Yesu.” Kukhala olimbika mu chisomo apa chikutanthauza kuti tiyenera kulimbitsa chikhulupiliro chathu mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu pokhulupilira mwa Iye ndi kukamira kwa Iye. Yesu Kristu anabwera ku dziko lino kuzatenga machimo athu onse kudzera mu ubatizo Wake, kufa pa Mtanda, anaukitsidwa ndi kukhala Mpulumutsi wathu. Ichi chikutanthauza kuti tiyenera kukhala olimbika mu chisomo cha Mulungu ndi kukhala oyamikira kwa Iye. Mulungu anatipulumutsa ife ndipo motero tiyenera kulola chipulumutso kudzera mu chikhululukiro cha machimo ngati mphatso ya Mulungu. Ichi ndi chipulumutso cha chikhululukiro cha machimo. Zilibe nazo ntchito ndi kupereka mapemphero a m’mawa a masiku onse kapena kusonkha ndalama za kumanga mpingo. Zinthu zonsezi zimaononga kwambiri osati zabwino kuti tilandire chipulumutso.
Chipulumutso chathu kudzera mu chikhululukiro cha uchimo chikutanthauza kuti Yesu Kristu, mosasamalira kanthu za zochita zathu, Iye anabatizidwa kuti anyamule machimo athu onse, kenako anafa pa Mtanda kuti achotse zolakwa zathu zonse. Iye anaukitsidwa kuti apulumutse ife ku machimo athu onse. Abusa amakhululukidwa ku machimo awo pokhulupilira mu uthenga wabwino oona umenewu, monganso anthu wamba. Aliyense amene amakhulupilira mwa Yesu Kristu motere ndi mtima wake onse amalandira chikhululukiro cha uchimo. Ndiyeno tingakhale ndi chilimbikitso mu chisomo cha chipulumutso ndi kulimbitsa chikhulupiliro chathu.
Ngati tikufuna moyo odzala ndi Mzimu Woyera, tiyenera kukhala olimba m’chikhulupiliro chathu mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Pali nthawi zina m’miyoyo yathu pamene timalephera kuyeza, ndipo timagwa m’kufoka kwathu. Ndi chifukwa chake tiyenera kukhala olimba mu chisomo cha chipulumutso. Nthawi zonse kulephera kwathu kumaoneka, tiyenera kuganizira bwino pa chikhulupiliro chathu mwa kunena pa ife tokha kuti, “Mulungu anandipulumutsa ine kudzera mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Yesu anandikhululukira machimo anga onse kudzera m’madzi ndi Mzimu.” Timakhala olungama mwa kukhulupilira mu uthenga wabwino umenewu ndi kuzilimbitsa tokha mwa kukhala ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Tinapulumutsidwa ku machimo athu onse ndi kukhala olimba pokhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Tinakhala anthu odalitsidwa kudzera mu chikhulupiliro chathu.
Paulo anati, “Cifukwa cace mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale mucita kanthu kena, citani zonse ku ulemerero wa Mulungu” (1 Akorinto 10:31). Ichi ndi chofunika kwambiri. Kutanthauza kuti tiyenera kuika miyoyo yathu kwa Mulungu. “mungakhale mudya, mungakhale mumwa.” Tiyenera kudya, kumwa ndi kukhala olimba kwa Mulungu kuti tichite ntchito Yake. Tiyenera kudya zinthu zabwino zathanzi lathu kuti tilalikire uthenga wabwino.
“Msilikari sakodwa nazo nchito wamba, kuti akakondweretse iye amene adamlemba usilikari.” (2 Timoteyo 2:4). Muyenera kukhala ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera pofuna kulalikira uthenga wabwino. Tingakhale ndi moyo wachikhulupiliro pamene tikukhala ndi moyo ofuna kulalikira uthenga wabwino. Onse amene amakhala ndi moyo wachikhulupiliro otere ndi odzala ndi Mzimu Woyera. Tiyenera tonse kubvutikira miyoyo yodzala ndi Mzimu Woyera. Ngakhale zopereka, zimene mumapeza chifukwa cha ntchito yanu yolimba, ziyenera kugwiritsidwa ntchito ku uthenga wabwino.
Ngati mukufuna kupitiriza ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera, muyenera kuzipereka nokha kwa Ambuye, khalani pa ntchito Yake, gwiritsani ntchito ndalama zanu pa uthenga wabwino ndi kugawana chimwemwe chanu chonse komanso zowawa ndi Mulungu. Ngati tikufuna kukhala umoyo otere, tiyenera kukhala m’chikhulupiliro ndi chifuniro cholimba kuti titumikire uthenga wabwino.
Anthu ambiri atsogoleredwa ndi umoyo wa iwo okha kufikira tsopano. Aika makoma ndi kupeza katundu wawo wa iwo okha mwa kukhala mbuye paokha. Komabe, tsopano tiyenera kukhala mwa Mulungu. Tiyenera kuona Mulungu ngati m’modzi wathu ndiponso Mbuye wathu Yekha. Ambuye anati, “Msilikari sakodwa nazo nchito wamba, kuti akakondweretse iye amene adamlemba usilikari.” Kukhala ndi moyo wa msilikali wabwino kukutanthauza kutsatira malamulo. Ambuye amakonza mavuto athu, amateteza ndi kutsogolera ife ngati tikukhala mwa Iye ngati asilikali Ake okhulupirika. Iye amatiuza kuti tithange tafuna Ufumu Wace choyamba ndi chilungamo Chake (Mateyu 6:33).
Mulibe chinthu chabodza m’mawu a Mulungu. Ngati titsatira Iye, tizaona choonadi cha mawu Ake. Koma kumbukirani kuti choyamba muyenera kukhala ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera mu mtima mwanu. Munthu amene alibe kukhazikika kwa Mzimu sangapereke ufumu wake kwa Mulungu. Koma, munthu amene ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera angapereke ufumu wake wa pa mtima kwa Mulungu ndipo motero angamvere kudzadzidwa kwa Mzimu Woyera ndi kupeza chimwemwe ndi mtendere mu mtima mwake.
Kukhazikika kwa Mzimu Woyera kudzachitika kwa inu pokhapo ngati mumvetsetsa ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. Ngati mukufuna kudzadzidwa ndi Mzimu Woyera ndipo mukufuna moyo odalitsidwa, muyenera kutumikira Mulungu ngati Mfumu ndi kukhala mu zabwino za Ufumu Wake. Ndiyeno muzadzadzidwa ndi Mzimu Woyera ndipo mtima wanu udzakhala ndi zambiri ndipo moyo wanu wapamwamba udzapitilirabe pamene mukupeza madalitso a kukhala ana mu Ufumu wa Mulungu.
Ndapereka uthenga kuti anthu amene analandira chipulumutso cha uchimo ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera pokhulupilira mwa Ambuye ayenera kukhala moyo odzala ndi Mzimu Woyera. Ndatanthauzira moyo odzala ndi Mzimu Woyera ndi kufotokoza m’mene moyo umenewu ungasungidwire. Ndafotokozanso kuti mwa chikhulupiliro muyenera kupereka mipando yanu yachifumu kwa Ambuye ndipo mwa chikhulupiliro muyenera kutumikira Iye ndi kusunga moyo odzala ndi Mzimu Woyera. .
Ndibwerezanso, kwa munthu amene ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera, kubadwa mwatsopano sikutha kwa zinthu. Ayenera kupitiriza kukhala umoyo odzala ndi Mzimu Woyera. Tiyenera kudziwa momveka bwino ndi kukhulupilira kuti mzimu ndi thupi zingadalitsidwe pokhapo ngati tikukhala moyo otere.
Moyo wotere sumachitika paokha. Umachitika pokhapo ngati takhulupilira mwa Ambuye ngati Mbuye wathu ndi kumuika pa udindo waukulu m’mitima yathu. Mulungu anatipulumutsa ndipo anatipatsa kale moyo odzala ndi Mzimu Woyera, moyo wotumikira uthenga wabwino. Iye anatipasanso ntchito Yake ndi udindo kuti tichite ntchito Yake, kuti tipitirizebe ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera.
Muyenera kuzipereka nokha kwa Iye ndi kukhala moyo mwa Iye. Tumikirani Iye polalikira uthenga wabwino okoma umenewu. Mtima wanu kenako udzadzadzidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo chimwemwe komanso chisomo chidzaturuka mwa inu. Patsiku la kubweranso Kwake, muzadalitsidwa, ndi kuimilira onyada pamaso pa Mulungu ndi kupata mphoto Zake. Inu ndi ine tiyenera kufunitsitsa moyo odzala ndi Mzimu Woyera. Tiyenera kulimba kuti tikhale ndi moyo otere kudzera mu chikhulupiliro. Umu ndi m’mene moyo odzala ndi Mzimu Woyera umasungidwira.
Kodi munausiya mpando wachifumu m’mitima yanu kuti mukhale ndi umoyo odzala ndi Mzimu Woyera? Ndikhulupilira kuti muzamulola Iye kuti atenge udindo waukulu kwambiri mu mtima mwanu. Muyenera kukhala ndi chifuniro chokhala ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera. Ndipomwepo pamene Iye adzakudalitsani kuti mukhale moyo odzala ndi Mzimu Woyera.