(Tito 3:1-8) “Uwakumbutse iwo agonje kwa akulu, ndi aulamuliro, akhale omvera, okonzeka pa nchito iri yonse yabwino; asachitire mwano munthu ali yense, asakhale andeu, akhale aulere, naonetsere cifatso conse pa anthu onse. Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akucitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundu mitundu, okhala m’dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzace. Koma pamene kukoma mtima, ndi cikondi ca pa anthu, ca Mpulumutsi wathu Mulungu zidaoneka, zosati zocokera m’nchito za m’cilungamo, zimene tidazicita ife, komatu monga mwa cifundo cace anapulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera, amene anatsanulira pa ife mocurukira, mwa Yesu Kristu Mpulumutsi wathu; kuti poyesedwa olungama ndi cisomo ca Iyetu, tikayesedwe olowa nyumba monga mwa ciyembekezo ca moyo wosatha. Okhulupirika mauwa, ndipo za izi ndifuna kuti ulimbitse mau, kuti iwo akukhulupirira Mulungu asamalire akhalebe atsogoleri a nchito zabwino. Izi nzokoma ndi zopindulitsa anthu.”
Kodi tingakhale bwanji ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera?
Tiyenera kumvetsetsa chifuniro cha Mulungu ndi kulalikira uthenga wabwino mogwirizana ndi iwo.
Iwo amene akhulupilira mwa Yesu ndipo ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera ayenera kukhala ndi moyo odzadzidwa ndi Mzimu Woyera. Kwa Akristu, moyo odzala ndi Mzimu Woyera ndi umene Mulungu amafuna. Tiyenera kutsatira malangizo Ake. Ndiyeno kodi tingakhale bwanji ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera? Tiyenera kumvetsera ku zimene Paulo ananena za chimenechi.
Kodi chofunikira ndi chiani kuti tikhale ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera
Mu Tito 3:1 Paulo anati, “Uwakumbutse iwo agonje kwa akulu, ndi aulamuliro, akhale omvera, okonzeka pa nchito iri yonse yabwino.” Choyamba pa zonse, anatiuza kuti tigonje kwa akulu ndi aulamuliro, timvere ndi kukhala okonzeka pa nchito yabwino. Chimene anatanthauza chinali chakuti sitingakhale ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera ngati sitimvera malamulo a dziko. Indedi, ngati aulamuliro a dziko ndi malamulo akulimbana ndi choonadi, sitiyenera kuti tiwamvere. Koma ngati malamulo sakuononga chikhulupiliro chathu, tiyenera kuwamvera kuti titumikire uthenga wabwino mwa mtendere.
Ife ndife amene tinalandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Kodi tingakhale motani ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera ngati tikuphwanya malamulo adziko? Choncho, kuti tikhale ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera, tiyenera kutsatira malamulo a dziko. Iwo amene analandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera ayenera kumvera miyambo yachikhalidwe. Tingayende ndi Mulungu pokhapo ngati tikusunga malamulo a dziko.
Tiyerekeze kuti wina wa ife wachita mlandu pa njira yopita ku mpingo. Kodi iye azatumikira Mulungu momasuka? Kodi angakhale motani padziko lino mogwirizana ndi ziphunzitso za Ambuye ngati akukhala kunja kwa lamulo? Sitiyenera kuononga miyambo yachikhalidwe pamene tikuyenda mu Mzimu. Palibe chabwino chimene chimabwera ngati taononga lamulo. Tiyenera kusunga mtendere kudzera mu kusunga lamulo. Tiyenera kuvutika kuti tikhale oongoka pamene tikulalikira uthenga wabwino. Kuti tikhale odzadzidwa ndi Mzimu Woyera, ndi kwa nzeru kwa oyera mtima kusunga malamulo a chikhalidwe.
Tiyenera kusunga umunthu mkati mwa mitima yathu
Paulo anati, “asachitire mwano munthu ali yense, asakhale andeu, akhale aulere, naonetsere cifatso conse pa anthu onse.” Kuti tikhale ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera, tisanene choipa kwa aliyense, tisakhale andeu, tionetse cifatso ndi kuonetsa umunthu kwa anthu onse.
M’mitima mwa iwo amene ndi obadwa mwatsopano, muli umunthu, chiletso ndiponso chifatso. Ichi ndi chotheka chifukwa cha Mzimu Woyera umene umakhala mwa ife. Paulo anatiuza ife kuti sitiyenera kuchepetsa uthenga wabwino pomenyana wina ndi mzake. Indedi, tiyenera kumenya pamene lamulo lachikhalidwe laukira uthenga wabwino. Koma pamene silinachite choncho, tiyenera kukhala mwamtendere. Tiyenera kupangitsa ena kuganiza za ife, “Ngakhale amaoneka oopsa ngati mkango nthawi zina, iye ndi wamtendere ngati nkhunda. Chikhulupiliro chake mu chi Mkristu mwina chimampangitsa kukhala odzichepetsa ndiponso munthu wanzeru.”
Mulibe chifatso kapena umunthu muzilakolako za thupi. Koma kudzera mwa kukhazikika kwa Mzimu Woyera ndiponso kudzera mwa Ambuye amene anatipulumutsa ife ku machimo athu, tingakhale ofatsa kwa ena. Kukhululukira wina amene wachita cholakwa chachikulu kwa ine ndi “chikhululukiro” chenicheni ndipo kumuona iye mwaumunthu kuchokera pansi panga pandekha ndi “umunthu” weniweni. siumunthu kunamizira kuti ndine wokoma mtima kwa wina pamene ndili ndi udani kwa iye. Kukhala ndi mtima odzala ndi umunthu ndi chikhululukiro ndi mkhalidwe la mkati kwa Akristu obadwa mwatsopano.
Tiyeneranso kukhala ndi chifatso pamene anthu atichitira zolakwa. Pokhapo ngati sakuyesa kutchingiriza uthenga wabwino, tiyenera kukhala ofatsa kwa aliyense. Koma ngati akutero, tiyenera kusinthanitsa kuunika kwa chifatso ndi kuunika kwa choonadi. Chifatso chimapezeka mu choonadi chokha cha Mulungu, kotero onse amene amatsutsa, kusokoneza kapena kunyoza mawu a Mulungu sayenera kuonetsedwa chifatso.
Mulungu sakhululukira iwo amene amatsutsa Iye koma amawapanga iwo kuti alipire mphoto. Mulungu anauza Abrahamu, “Ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe” (Genesis 12:3). Anthu amene amatsutsa uthenga wabwino wa choonadi alibe njira yakuti azapulumutsidwa. Iwo sadzakwanitsa kupewa chionongeko chimene chidzaononga osati miyoyo yawo yokha koma mibadwonso yonse yachitatu ya makolo awo.
Kodi ndi chifukwa chiani tiyenera kukhala opilira ndiponso odzichepetsa? Monga kunalembedwa mu Tito 3:3, “Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akucitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundu mitundu, okhala m’dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzace.” Tinali ngati anthu amenewa tisanabadwe mwatsopano. Choncho tiyenera kulolera ndi kuwakhululukira chifukwa poyamba tinali ngati iwo.
Mu Tito 3:4-8, akunena kuti, “Koma pamene kukoma mtima, ndi cikondi ca pa anthu, ca Mpulumutsi wathu Mulungu zidaoneka, zosati zocokera m’nchito za m’cilungamo, zimene tidazicita ife, komatu monga mwa cifundo cace anapulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera, amene anatsanulira pa ife mocurukira, mwa Yesu Kristu Mpulumutsi wathu; kuti poyesedwa olungama ndi cisomo ca Iyetu, tikayesedwe olowa nyumba monga mwa ciyembekezo ca moyo wosatha. Okhulupirika mauwa, ndipo za izi ndifuna kuti ulimbitse mau, kuti iwo akukhulupirira Mulungu asamalire akhalebe atsogoleri a nchito zabwino. Izi nzokoma ndi zopindulitsa anthu.”
Malingana ndi Baibulo, Mulungu sanatipulumutse ku machimo athu chifukwa tinachita ntchito zabwino. Iye anatipatsa madalitso a kubadwa mwatsopano chifukwa anatikonda ndi kutimvera chisoni. M’mawu ena, Yesu Kristu anabwera ku dziko lino, anabatizidwa, kufa pa Mtanda, anaukitsidwa, ndipo motero anatsuka machimo athu onse. Yesu anaukitsidwa ndipo tsopano akukhala kudzanja la manja la Mulungu. Mwa kuukanso kwa akufa, zinthu zonse zosamalizika m’dziko lino zinakhala zangwiro.
Mulungu anatidalitsa ndi Mzimu Woyera kudzera mwa Yesu Kristu Mpulumutsi wathu. Yesu Kristu anabatizidwa ndi Yohane kuti achotse machimo onse a dziko ndi kufa pa Mtanda ndi cholinga choti machimo athu onse akhululukidwe. Tinapulumutsidwa ndipo tinakhala olungama.
Baibulo limanenanso kuti, “Tikayesedwe olowa nyumba monga mwa ciyembekezo ca moyo wosatha.” Ichi chikutanthauza kuti ife, monga cholowa cha Mulungu, ndife amene tinalowa mu chuma chonse ndi ulemerero Wake. Kuti tikhale moyo wodalitsika umenewu, tiyenera kukhala ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera. Muyenera kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, kukhululukidwa machimo anu onse ndi kulalikira uthenga wabwino kwa ena.
Choncho, titakhululukidwa ku machimo athu onse, tiyenera kugwilira ntchito ena kuti apindule, tiyenera kusunga malamulo a dziko ndi kulalikira uthenga wabwino kwa iwo amene akufunafuna Mulungu. Ndipo Tiyenera kukhululukira anthu amene atichitira ife cholakwika ndi kuwachitira zabwino ndiponso umunthu kotero kuti asasokoneze kulalikira kwa uthenga wabwino okoma. “Izi nzokoma ndi zopindulitsa anthu.” Ngati mukufuna kudzadzidwa kwa Mzimu Woyera, muyenera kukumbukira zimene Paulo ananena kwa ife. Ichi sichingamveke ngati chinthu chapamwamba, koma ndi mawu ofunikira kwambiri.
Popeza tikukhala m’dzikoli, sitingadzadzidwe ndi Mzimu Woyera ngati tili mu mkangano ndi ena posamvera malamulo a dziko lino. Motero tiyenera kumvera malamulo pokhapo ngati sakulimbana ndi mawu a Mulungu. Tiyenera kumvera malamulo a dzikoli. Ngakhale kuti tili ndi chikhulupiliro, kumvera malamulo ndi chisankho chabwino ngati tikufuna kukhala ndi miyoyo yodzala ndi Mzimu Woyera. Kuti ife tichite ntchito zabwino, tiyenera kumvera malamulo a dziko ndi kukhalira pamodzi ndi oyandikana nafe.
Kodi mukufuna kukhala ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera?
Aefeso 5:8-11 anena kuti, “Pakuti kale munali mdima, koma tsopano muli kuunika mwa Ambuye; yendani monga ana a kuunika, pakuti cipatso ca kuunika ticipeza m’ubwino wonse, ndi cilungamo, ndi coonadi, kuyesera cokwenderetsa Ambuye nciani; ndipo musayanjane nazo nchito za mdima zosabala kanthu, koma maka-makanso muzitsutse.” Ndimeyi ikutiuza kuti tiyende ngati ana a kuunika ndi kubala zipatso za Mzimu.
Motero Aefeso 5:12-13 akunena kuti, “pakuti zocitidwa nao m’tseri, kungakhale kuzinena kocititsa manyazi. Koma zinthu zonse potsutsika ndi kuunika, zionekera; pakuti conse cakuonetsa ciri kuunika.” Paulo akunena apa kuti zinthu zonse zionekera potsutsika ndi kuunika. Ngati munthu olungama sangakhale mwachilungamo, adzaonetsedwa mwina ndi Mulungu kapena iye mwini. Kodi chimachitika ndi chiani ngati munthu wapezeka akuchita ntchito za mdima, ndipo kenako wadzudzulidwa ndi kuunika? Pamene wavomereza zolakwa zake, mtima wake umaunikiridwa pamene wakumananso ndi Mulungu. “Koma zinthu zonse potsutsika ndi kuunika, zionekera; pakuti conse cakuonetsa ciri kuunika.” N’kwabwino kuonetsedwa ndi kuunika. Ndiyeno tingavomereze zolakwa zathu ndi kubwerera kwa Mulungu.
Ngati tikufunadi kukhala ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera tiyenera kukhala ndi chifundo m’mitima yathu. Ngakhale kuti wina wake alibe uchimo mu mtima mwake, sichikutanthauza kuti sayenera kukhala wachifundo. Tiyenera kukhala ndi ubwino ndiponso chifundo m’mitima yathu. Tiyenera kulalikira ndi nzeru ndi kupempherera anthu amene sakudziwa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu kotero kuti amvetsetse uwo ndi kukhululukidwa ku machimo awo. Ndipo sitiyeneranso kuononga ena. Tiyenera kudya, kugona ndi kukhalira uthenga wabwino ndi kutumikiranso ena.
Kukhala ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera, tiyenera kuganizira za kufunika kwa nthawi ndi kutumikira uthenga wabwino okoma ngati anthu anzeru. Pamene tikonda dziko, timakhala pansi pa chinyengo cha mdima ndipo tizanyalanyaza ntchito ya Mulungu. Motero, tiyenera kuyang’ana maso athu pa Ambuye ndi kuchita zimene Iye akufuna. Pamene tikukhulupilira mu chipulumutso chimene Mulungu anatipatsa, tiyeneranso kukhala maso nthawi zonse. Munthu wanzeru wa Mzimu ayenera kuzipereka kukulalikira uthenga wabwino okoma dziko lonse dziko lisanadzadzidwe ndi mdima.
Mvetsetsani chifuniro cha Ambuye
Tiyenera kuyesa kupeza chimene chimakondweretsa Mulungu. Tiyenera kuphunzira zimene Iye akufa kuti ife tichite kudzera mu mpingo ndiponso mawu Ake. Tiyenera kudziwa chimene tingachite kuti tikondweretse Mulungu ndi kuchita chifuniro Chake kwa ife.
Anthu amene anakhululukidwa machimo awo ndi amene abadwa mwatsopano ndipo ndi okhawo amene abadwa mwatsopano amene ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Iwo amene ali ndi Mzimu Woyera mkati mwawo ndi anthu oyeradi ndiponso ana a Mulungu. Ayenera kukhala ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera. Iyi ndi ntchito ya oyera mtima onse. Sitiyenera kuononga khama lathu ndi mphamvu zathu pa ife tokha, mosiyana ndi zofuna za ena. Sitiyenera kutsekereza ntchito za Mulungu mwa poyenda pamodzi ndi kusintha kwa nthawi.
Ngati tinayeretsedwa ndi kulandira kubadwanso kudzera mu chikondi cha Mulungu, tiyenera kukhala munthu wabwino kuti tipitirize ndi kugwira ntchito Yake. Ngati takhala ana a Mulungu pokhulupilira mwa Iye, ndi kwabwino kwa ife kukhala anthu ochita zabwino.
Thupi la ana a Mulungu lili kutali ndi ungwiro koma limasangalatsa Mulungu; pokhapokha ngati tiri okhudziwa ndi chifuniro cha Mulungu ndi kuchita zabwino. Koma ngakhale iwo amene ndi obadwa mwatsopano angachite zoipa kwa ena ngati akukhala chifukwa cha iwo okha. “Ndipo musaledzere naye vinyo, m’mene muli citayiko; komatu mudzale naye Mzimu” (Aefeso 5:18) kutanthauza kuti sitiyenera kukhala oledzera ndi zilakolako za thupi koma tiyenera kuchita ntchito zabwino.
Paulo ananena mu Aefeso 5:19-21, “Ndi kudzilankhulira nokha ndi masalmo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuyimbira ndi kuyimba m’malimba Ambuye mumtima mwanu; ndi kuyamika Mulungu Atate masiku onse, cifukwa ca zonse, m’dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu; ndi kumverana wina ndi mnzace m’kuopa Kristu.” Ngati tikufuna kukhala ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera, tiyenera kukhulupilira ndi kulalikira uthenga wabwino wa chipulumutso ndi kuvumbulutsa zimene Mulungu wachita kwa ife.
Mulungu amatidalitsa nthawi zonse pamene tikupemphera ndipo walemba madalitso onsewa m’masalmo ndi m’malimba komanso nyimbo za uzimu kuti ife timtamande m’mawu amodzi. Tiyenera kuyamikira, kuthokoza ndi kumutamanda Iye. Tingakhale ndi miyoyo yodalitsika yodzala ndi Mzimu Woyera pamene tikupempherera iwo amene asanapulumutsidwe ndi kwa wina ndi mnzake. Tiyenera kuthokoza Mulungu kuchokera pansi pa mitima yathu ndi kulemekeza Yesu Kristu, amene anatipulumutsa ife. Ndi maganizo amenewa m’mitima yathu, tiyenera kuvomereza zolakwa zathu, kuonetsa chiyamiko chathu choyeretsedwa machimo athu ndi kumulemekeza. Ichi ndi chimene chikutanthauza kukhala wodzadzidwa ndi Mzimu Woyera.
Tiyenera kutumikira uthenga wabwino okoma miyoyo yathu yonse
Tiyenera kukonza ntchito zabwino ndi kuzitsata chifukwa cha ulemelero waukulu wa uthenga wabwino okoma. Kukhala olumikizana ndi mpingo wa Mulungu, tiyenera kupemphera pamodzi ndi kuitana pa Mulungu kuti apulumutse miyoyo ya aliyense. Padakali anthu ambiri amene asanabadwe mwatsopano chifukwa sakudziwa uthenga wabwino okoma ngakhale kuti afunafuna Mulungu. Tiyenera kupempherera anthu amenewa, kunena kuti, “Mulungu, chonde naonso apulumutseni.” Ndipo sitifunika kutsata zinthu zozikonda tokha koma kupereka katundu wathu mu kutumikira uthenga wabwino kuti tipulumutse osochera. Kukhala chifukwa cha miyoyo ya ena ndi kukulitsa Ufumu wa Mulungu ndi kuchita ntchito yabwino.
Kuchita ntchito yotere kukutanthauza kukhala ndi moyo wodzala ndi Mzimu Woyera. Kukhala ndi kudzadzidwa kwa Mzimu Woyera sikutanthauza kukhala ndi kuthekera kolankhula m’malilime ndi kuchita zozizwitsa, koma kuphunzira m’mene tingakondweretsere Mulungu. Kukuutanthauza kukhulupilira mu chipulumutso chimene Mulungu anatipatsa ife, kutamanda ndi kupatsa ulemerero Mulungu m’ndakatulo komanso m’masalmo. Kuthokoza, kutamanda ndi kulemekeza Mulungu ndi mtima wathu onse, ndi kumtumikira Iye ndi matupi athu ngati ziwiya za chilungamo ndi chifuniro cha Mulungu. Kutsatira malamulo ake kukutanthauza kukhala ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera.
Kukhala ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera, tiyenera kulemekezana wina ndi mzake. Ngati munthu akutipatsa ife langizo, tiyenera kumvetsera ku zimene akunena. Mwa njira yomweyi, ngati ndapereka langizo kwa iye, ayenera kumvetsera ngakhale kuti sagwirizana nane. Chimodzimodzi, tiyenera kukhala ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera pomverana wina ndi mnzake ndi kuchita ntchito ya Mulungu.
Kukhala ndi moyo odzala ndi Mzimu kukutanthauza kulemekeza Yesu Kristu
Kukhala ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera kukutanthauza kusunga malamulo a Yesu Kristu. Tiyeni tione zomwe chimenechi chikutanthauza powerenga Aefeso 6:10-13. “Cotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m’kulimba kwa mphamvu yace. Tabvalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kucirimika pokana macenjerero a mdierekezi. Cifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akucita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi a uzimu a coipa m’zakumwamba. Mwa ici mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima citsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutacita zonse, mudzacirimika.”
Kodi chikutanthauza chiani kukhala ndi moyo odzadzidwa ndi Mzimu Woyera? Chikutanthauza kukhala olimbika mwa Ambuye ndi kukhala ndi chikhulupiliro mu mphamvu Yake. Kutanthauza kukhala mwa mphamvu za Mzimu Woyera umene umakhala mwa ife ndipo osati mwa chifuniro chathu chokha. Kuonjezerapo, kukutanthauza kukhala ndi moyo wa mapemphero. Mwa kupemphera, tingakhale ndi moyo wamphamvu kulandira maluso osiyanasiyana ndi madalitso amene Mulungu anatipatsa. Kukhala ndi moyo otere kukutanthauza kuvala zida zonse za Mulungu. Ndife ofoka kwambiri kotero kuti ngakhale timayesa kuyenda ndi Iye, kutumikira ndi kumvera Mulungu, sitingakhale ndi moyo odzala ndi Mzimu ngati sitigwira pa mawu Ake.
Chikhulupiliro m’mawu a Mulungu ndi chofunika kuti tiwonjezere mphamvu zathu za uzimu. Ngakhale kuti tili ndi chikhulupiliro, tiyenera kuvala zida zonse za Mulungu mwa kunena kuti, “Ndili ndi chitsimikizo choti zidzakhala monga zinalembedwa m’mawu a Mulungu.” Ichi ndi chikhulupiliro chimene chimapangitsa ife kukhala ndi moyo odzadzidwa ndi Mzimu Woyera.
Kodi aliyense wa inu ali ndi vuto lokhala ndi moyo otere? Ndiyeno kumbukirani mawu a m’Malembo ndipo valani zida zonse za Mulungu. Mulungu anatiuza kuti tivale zida Zake zonse. Potenga mawu ndi kusunga mkati mwa mtima wanu, muzaphunzira kuti kuvala zida zonse za Mulungu kukutanthauza chiani. Mosasamala kanthu za nyengo zathu ndi zimene anthu akunena, tiyenera kukakamira ku mawu a Mulungu. Mwa njira imeneyi, tizakhala ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera.
Kodi chikhulupiliro chimenechi tingachitenge kuti? Chivumbulutso 3:22 akunena kuti, “Iye wakukhala nalo khutu amve cymene Mzimu anena kwa Mipingo.” Tiyenera kumvera ku zimene Mzimu ukunena ku mpingo. M’mawu ena, sitingamvere mawu a Mulungu kapena kukhala ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera koma kukhala akapolo a Mulungu. Kodi Mzimu Woyera umayankhulira kudzera mwa ndani? Mulungu amalankhula kwa oyera mtima ndi anthu onse adziko lapansi kudzera mwa atumiki Ake komanso mpingo Wake.
Uko ndi kunena kuti, muyenera kukhulupilira kuti ziphunzitso zampingo wa Mulungu zoonadi zimachokera m’mawu a Mulungu. Muyenera kuvomereza ziphunzitso za mpingo ndi chikhulupiliro chimenechi m’maganizo. Ngati Mzimu Woyera sunakhale mwa olalikira, kungakhale kotheka kuti iye aphunzitse za m’maganizo mwake. Mlaliki amene ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera amalalikira mawu a Mulungu motsogozedwa ndi Mzimu Woyera. Ngati samachita motero koma kulalikira mawu a m’Baibulo opanda tanthuzo, Mzimu Woyera umamuletsa chifukwa umakhala mu mtima mwake.
Mzimu Woyera ndi Mulungu. Ulamuliro wa atumiki a Mulungu ndi opambana kwambiri chifukwa Mulungu amakhala mwa iwo. Mu Chipangano Chatsopano, Yesu Kristu ananena kwa Petro “Ndidzakupatsa mafungulo a Ufumu wa Kumwamba” (Mateyu 16:19). Mafungulo a Kumwamba ndi uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. M’mawu ena, uthenga wabwino umenewu ndi fungulo lolowera Kumwamba. Mulungu anapereka ulamuliro wa kulalikira mawu a Mulungu osati kwa Petro yekha koma kwa kapolonso aliyense wa Mulungu ndi oyera mtima onse, pokhapo ngati ali obadwa mwatsopano ndi kukhala ndi Mzimu Woyera.
Kuti tikhale ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera, tiyenera kuvala zida zonse za Mulungu. Ngati tilibe chikhulupiliro, tiyenera kusunga ziphunzitso za mpingo m’maganizo mwathu masiku onse pokhulupilira mu ulamuliro wa mpingo ndi mwa akapolonso a Mulungu. Ngakhale kuti ulaliki umene mwamva lero ulibe ntchito ndipo sukugwirizana ndi moyo wanu, muyenera kuumvera mwanjira iliyonse ndi kuuika mu mtima mwanu. Pezani mawu m’Baibulo amene ali ofunika mu moyo wanu wa masiku onse. Kakamirani pa iwo. Mwa njira imeneyi, muzakhala munthu wachikhulupiliro. Ndiyeno muzatha kukhala ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera, kuyenda ndi Mulungu ndi kupambana nkhondo kwa akulu ndi aulamuliro a mdima a m’dziko lapansi.
Mungasokonezeke chifukwa munauzidwa kuti muyenera kumvera aulamuliro a dziko lapansi koma tsopano ndikunena kwa inu kuti muyenera kumenyana ndi aulamuliro a mdima a dziko lapansi. Mu nthawi ya Aroma, Mfumu ya Aroma inkazitcha yokha kuti ndi Mulungu ndipo lamulo linafuna kuti anthu onse azimuona ngati Mulungu. Koma ichi chinali chinthu chimene Akristu sakanachita chifukwa chinali chosemphana ndi mawu a Mulungu. Choncho Akristu mu nthawi imeneyo analibe chisankho koma kumenyana ndi Mfumu ya Aroma, amene anapangitsa anthu kugwadira iye ngati kuti anali Mulungu.
Kuti tipambane nkhondo ndi mdierekezi, tiyenera kukhulupilira ndi kukakamira ku mawu a Mulungu. Ngati tidzakhala mogwirizana ndi mawu a Mulungu, tizapeza madalitso ake ndi kukwanitsa kugonjetsa mdierekezi. Ngakhale kuti tapulumutsidwa, tizagonja kunkhondo ya Satana ngati sitikakamira ku mawu a Mulungu. Mulungu akutichenjeza, “Mdani wanu mdierekezi, monga nkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire” (1 Petro 5:8). Munthu amene sakhulupilira m’mawu a Mulungu amagwidwa mosavuta ndi mdierekezi.
Ngakhale Yesu sakanatha kumenyana ndi Satana kukanakhala kuti mawu a Mulungu kunalibe. “Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mau onse akuturuka m’kamwa mwa Mulungu” (Mateyu 4:4). Iye anathamangitsa mdierekezi kudzera m’chikhulupiliro chimene chinalembedwa. Ndipo nanga bwanji ife? Ndife osoweka nzeru ndipo ndife osiyana ndi Yesu. Motero, tiyenera kukhulupilira ndi kukakamira kwambiri ku mawu a Mulungu.
Sitiyenera kungonena kuti, “Ndikuganiza kuti mawu ndi oyenera koma sindingakhulupilire mwa iwo kwathunthu.” Tiyenera kukakamira pa mawu. “Ndikhulupilira kuti zinthu zonse zizatembenuka kukhala zoona monga m’mene zinalembedwera.” Ichi ndi chikhulupiliro choyenera ndipo chimatilola kuvala zida zonse za Mulungu. Anthu amene amanena kuti, “Zinthu zonse zidzazindikiridwa ndendende monga m’mene Ambuye ananenera” adzadalitsidwa. Ngati munthu akukakamira ku mawu a Mulungu ndi kudalira pa iwo, zinthu zizasintha kukhala zabwino mogwirizana ndi chikhulupiliro chake. Ngakhale kuti mdierekezi amafuna kutiyesa, iye adzachoka ngati tinganene kuti, “Ndimakhulupilira m’mawu a Mulungu. Ndikhulipilira kuti mawu Ake ndi mayankho olondola.” Iyi ndi njira yopambanira nkhondo ya mdierekezi.
Tiyenera kukakamira pa mawu a Mulungu
“Mwa ici mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima citsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutacita zonse, mudzacirimika. Cifukwa cace cirimikani, mutadzimangira m’cuuno mwanu ndi coonadi, mutabvalanso capacifuwa ca cilungamo; ndipo mutadzibveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere; koposa zonse mutadzitengeranso cikopa ca cikhulupiriro, cimene mudzakhoza kuzima naco mibvi yonse yoyaka moto ya woipayo. Mutengenso cisoti ca cipulumutso ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mau a Mulungu ” (Aefeso 6:13-17).
Mu ndimeyi, “Cifukwa cace cirimikani, mutadzimangira m’cuuno mwanu ndi coonadi,” mawu a Mulungu afanizidwa ndi lamba lomangidwa m’chuuno cha munthu. Ichi chikutanthauza kuti tiyenera kumanga maganizo athu ndi mawu Mulungu. Iye akutiuza kuti titsatire mawu a choonadi kuti tikhale pamodzi m’maganizo ndi Mulungu. Koma pamene lambali likugwira molimba kuzungulira thupi, tiyenera kuzimanganso molimba ku mawu a Mulungu. Pamene tili amodzi m’maganizo ndi Mulungu, mwachilengedwe tizakwanitsa kukhulupilira ndi kunena kuti, “Ndikhulupilira kuti zinthu zonse zizakhala bwino. Ndili ndi chitsimikizo kuti zonse zidzazindikiridwa monga Mulungu ananenera.”
Chotsatira, tiyenera kuvala chapachifuwa cha chilungamo. Tiyenera kuvala chapachifuwa cha uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu chimene chimanena kuti Mulungu watipulumutsa ife. Tiyenera kuvala lamba m’chiuno mwathu la choonadi, titavala chodzitetezera chapachifuwa cha chilungamo. Tiyenera kuvala chapachifuwa cha miyala ya mtengo wapatali. Tiyenera kuzivala ndi chikhulupiliro chakuti Mulungu anatikhululukira machimo athu onse. Tiyenera kukhulupilira mawu a Mulungu ndi mtima wathu onse. Tiyeneranso kulalikira uthenga wabwino wa chipulumutso umene umapatsa mtendere.
Titakamira ku mawu onse ali pamwamba, tiyenera kuvala nsapato ndi kukonzekera kwa uthenga wabwino wamtendere, ndi kupita kukalalikira uthenga wabwino wachipulumutso umene umapatsa mtendere wa Mulungu kwa anthu onse. Ngati tinapulumutsidwa ku machimo athu onse, timavomereza chikhululupiliro chathu kudzera ndi pakamwa pathu. Ndipo nthawi zonse pamene uchimo wathu ndi kuipa zavumbulutsidwa, tiyenera kuzifufuta posinkhasinkha pa choonadi chimene Mulungu anakhululukira kale machimo athu onse. Iye anachita choncho kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake pa Mtanda. Tiyenera kukhala ndi moyo waulemelero kudzera mu kuthokoza Mulungu. Tiyenera kulalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu, umene umapatsa mtendere kwa aliyense amene sanaomboledwe ku machimo ake.
Pa zonse, tiyenera kumenyana ndi oipa ndi chishango cha chikhulupiliro. Pamene Satana waukira, tiyenera kumuthamangitsa ndi chishango cha chikhulupiliro ku dzanja limodzi ndi mawu a choonadi kudzanja lina.
Ndiyeno tiyenera kuvala chisoti cha chipulumutso. Tiyenera kulola mawu a chipulumutso, kunena kuti, “Ndinapulumutsidwa ku machimo anga onse kudzera mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Mulungu anakhululukira machimo anga m’njira imeneyi.” Tiyenera kuzindikira choonadi m’mutu mwathu. Tiyenera kupanga mawu a Mulungu, chisoti cha chipulumutso ndi lupanga la Mzimu kukhala zida zathu polimbana ndi mdierekezi
Ngati Satana watiukira ife, tiyenera kusolola lupanga ndi kum’menya nalo. “Mulungu ananena ichi! Ndipo ndikukhulupilira kuti ziri choncho. “Timathamangitsa Satana kudzera mu chikhulupiliro m’mau a Mulungu. Ngati tikhulupilira m’mawu a Mulungu ndi kusolola lupanga lanu lauzimu, Satana adzathawa akufuula “Ouchi! Zikuwawa bwanji.” Tingagonjetse kuukira konse kwa Satana pokhapo ngati tikhulupilira mu mawu a Mulungu.
Tiyenera kukhala ndi moyo otere obvomereza kuti, “Thupi langa lili kutali ndi ungwiro, koma ndine munthu wa Mulungu amene ndinalandira chiombolo. Ndimakhala mwa chikhulupiliro, kukakamira ku mawu amene Mulungu anandiuza ine.” Ngati tili ndi chikhulupiliro chotere, tingathamangitse Satana ndi lupanga la choonadi nthawi zonse ngati wabwera kuzatizunza ife ndi kusokoneza miyoyo yathu chikhulupiliro. Satana samaphethira ngati tamuyandikira ndi mawu chabe a dziko. Motero, tiyenera kumenya iye ponena kuti, “Ichi ndi chimene Mulungu ananena.” Kenako Satana adzagonja pamaso pa ulamuliro wa mawu a Mulungu.
Ngati tikufuna kukhala ndi umoyo odzala ndi Mzimu Woyera, tiyenera kupemphera kwa Mulungu kuti mpingo, oyera mtima onse ndi akapolo a Mulungu adzipereke okha kukulalikira uthenga wabwino. Ponena pemphero monga, “Ndiloleni molimba mtima ndivumbulutse zinsinsi za uthenga wabwino,” tizakhala ndi moyo ofuna kutumikira uthenga wabwino. Uwu ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera. Kukhala ndi moyo wodzala ndi Mzimu Woyera ndi ofunika kwa oyera onse. Ngati tikufuna kukhala oyera oona, tiyenera kukhala ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera. Kukhala ndi moyo otere ndi kofunikira kwa oyera mtima onse, monga momwe kulandira chikhululukiro cha machimo kuli kofunikira ku moyo ulionse. Ili ndi lamulo la Mulungu.
Iwo amene anapulumutsidwa ku machimo awo koma sadziwa m’mene ayenera kukhalira moyo wao wachikhulupiliro ayenera kudziwa kuti ayenera kukhala ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera. Ichi ndi chimene Mulungu akufuna. Oyera mtima ayenera kukhala ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera, umene ndi chifuniro cha Mulungu. Moyo odzala ndi Mzimu Woyera umalimbikitsa oyera mtima kulalikira uthenga wabwino pochita ntchito yabwino. Iwo amakonda kulalikira uthenga wabwino, kupemphera kwa Mulungu, ndi kukhulupilira ndiponso kukakamira pa mawu a Mulungu. Tiyenera kuvala chisoti cha chipulumutso ndiponso chapachifuwa cha chilungamo ndi kuthamangitsa Satana mwa kunena kuti, “Ndine olungama nthawi zonse.”
Popeza oyera mtima ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera, amayenda mu Mzimu ndipo amatha kulandira mphamvu za Mzimu Woyera. Iwo akuchita ntchito Yake ndi madalitso a Mulungu omwe anapezeka kuchokera ku pemphero la chikhulupiliro. Ndipo ayenera kuyenda mu Mzimu kufikira pamene adzagonjetsa satana ndi kuima pamaso pa Mulungu. Anthu amene angavale zida zonse za Mulungu ndi Akristu obadwa-mwatsopano okha amene angakhale ndi moyo odzadzidwa ndi Mzimu Woyera.
“Cifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akucita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi a uzimu a coipa m’zakumwamba” (Aefeso 6:12). Nkhondo ya iwo amene ndi obadwa mwatsopano sinkhondo yathupi ndi mwazi. Komabe, nkhondo ya iwo amene ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera ndi yolimbana ndi zinthu zauzimu zoipa ndi iwo amene amatsekereza miyoyo yathu yachikhulupiliro, satumikira uthenga wabwino ndipo amatisokoneza.
Pamene tikupita kukamenya nkhondo yauzimu ya uthenga wabwino wa Ambuye, tiyenera kuvala chisoti ndi zida za Mzimu. Ngati tingavale zovala zathu zanthawi zonse mu nkhondo imeneyi, tizavulazidwa. Motero, tiyenera kuvala zida zankhondo. Tifunika malupanga, zishango ndi zisoti. Kuti tipambane nkhondo, tiyenera kukonzekera bwino nkhondo isanachitike. Tiyenera kuvala chapachifuwa, kumanga lamba m’chuuno, ndi kuvala nsapato ku mapazi onse. Kenako, ndi lupanga komanso chishango ku manja athu onse, tiyenera kugonjetsa adani athu. Uwu ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera.
Tiyenera kusunga uthenga wabwino okoma
Paulo anatiuza ife, “Cosungitsa cokomaco udikire mwa Mzimu Woyera amene akhalitsa mwa ife” (2 Timoteyo 1:14). Kodi chosungitsa chokoma ndi chiti? Ndi uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu umene unapulumutsa ife ku machimo athu. Mu Tito 3:5 akunena kuti, “Komatu monga mwa cifundo cace anapulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera.” Ambuye wathu anatsuka machimo onse amene tinachita mu dziko lino, anafa pa Mtanda ndipo anaukitsidwa. Tiyenera kusunga uthenga wabwino okoma umenewu. Tiyenera kuvala chisoti cha chipulumutso ndi chapachifuwa cha chilungamo ndi kuvala lamba m’chuuno mwathu ndi choonadi. Tiyenera kukhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu.
Mwa kuzikonzekeretsa tokha m’njira imeneyi, tiyenera kupambana nkhondo yolimbana ndi Satana. Pokhapo ndi pamene tidzakwanitsa chigonjezo ndi kugawana ndi ena. Tiyenera kumenya nkhondo zauzimu zambiri molimbana Satana ndi kunyamula mphoto zambiri kuchokera kwa iye kufikira tsiku limene tikalowe mu Ufumu wa Ambuye, omwe ndi cholowa chathu. Pamene tapambana ndewu zambiri molimbana ndi mdani wathu ndipamenenso ndewu yotsatira imakhala yosavuta. Tonse tiyenera kupempherera Ufumu Wake kuti uchite bwino ndi kuchuruka. Kenako tingapeze moyo odzala ndi Mzimu Woyera.
Sitiyenera kukhala okhutitsidwa ndi kukhululukidwa kwa machimo athu koma tiyenera kukhala moyo odzala ndi Mzimu Woyera. Chifukwa cha uthenga wabwino ndi ntchito zathu zabwino, tiyenera kukhulupilira m’mawu a Mulungu. Tiyenera kutsogoleredwa ndi Mzimu Woyera ndi kukhala osunga mawu a Mulungu ndi kukhulupilira mwa iwo, kotero kuti tisalephere ndewu ndi Satana ndi kuonongedwa.
Kodi mukundimvetsetsa ine? Pokhapo ndi pomwe tingakhale ndi miyoyo yodzala ndi Mzimu Woyera. Ndili ndi chiyembekezo kuti inunso mudzatumikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndi kuudalira ndiponso kutsatira mawu a Mulungu. Tiyeni tonse tichite ntchito ya kupulumutsa miyoyo kwa Satana. Tingakhale ndi miyoyo yodzala ndi Mzimu Woyera kufikira pamene Ambuye adzabweranso. Kuti tilandire kudzadzidwa kwa Mzimu Woyera ndi lamulo lachiwiri limene Mulungu anapereka kwa ife. Thokozani Iye. Tingakhale ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera chifukwa cha chikhululukiro cha machimo m’mitima mwathu. Kukanakhala kuti sikunali chifukwa cha kukhazikika kwa Mzimu Woyera, sindikanayamba moyo odzala ndi Mzimu Woyera. Ndikuthokoza Mulungu pakutilola kuti tikhale ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera.
Kodi mukhulupilira kuti muli ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera? Kwa iwo a ife amene tinakhululukidwa machimo athu, tiri ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Koma iwo amene asanafufute machimo awo sanakhalebe ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Iwo amene sakudziwa kapena sakhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu alibe kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Anthu onse m’dziko adzaponyedwa ku Gehena ngati alibe kukhazikika kwa Mzimu Woyera.
Popeza tilibe uchimo mu mitima yathu, tili ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera. Ndipo chifukwa chakuti Mzimu Woyera umakhala m’mitima yathu, tingakhale ndi moyo odzala ndi Mzimu Woyera. Ife, amene tili ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera, tiyenera kumvera khumbo la Mzimu kuti tidzadzidwe ndi Mzimu Woyera. Pamene tikumvera kwambiri khumbo la Mzimu, ndi pamene chikhulupiliro chathu chimalimba ngati wankhondo ali ndi zozitetezera zonse. Koma ngati talephera kumvera Mzimu, ndi chimodzimodzi kuti ife tabvula zida zankhondo.
Tiyeni tikule kudzera m’mawu a Mzimu Woyera ndi kukhala munthu wachikhulupiliro. Pamene tamvera mawu a Mzimu Woyera, chikhulupiliro chathu chimakula chifukwa Mulungu amati “Comweco cikhulupiriro cidza ndi mbiri, ndi mbiri idza mwa mau a Kristu.” (Aroma 10:17). Motero, ngakhale kuti Satana atiukire, ndife otetezedwa ndi chikhulupiliro chathu m’mawu amenewa. Satana sangaukire iwo amene akonzekera zida zankhondo ndi chishango cha chikhulupiliro pokhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Anthu okhulupirika ali ndi mphamvu yodziteteza kuukira kwa Satana ndi chikhulupiliro chawo.
Tiyeni tikhale moyo odzala ndi Mzimu Woyera ndi chikhulupiliro. Moyo odzala ndi Mzimu Woyera ukuimira moyo olalikira uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu mwa chikhulupiliro padziko lonse lapansi. Otere ndi moyo wodzala ndi Mzimu Woyera.