• All e-books and audiobooks on The New Life Mission website are free
  • Explore multilingual sermons in global languages
  • Two new revised editions in English have been released
  • Check out our website translated into 27 languages
Search

Sermons

Mutu 8: Mzimu woyera

[8-13] Ntchito ndi Mphatso za Mzimu Woyera (Yohane 16:5-11)

Ntchito ndi Mphatso za Mzimu Woyera(Yohane 16:5-11)
“Koma tsopano ndimuka kwa Iye wondituma Ine; ndipo palibe wina mwa inu andifunsa Ine, Munka kuti? Koma cifukwa ndalankhula izi ndi inu cisoni cadzala mumtima mwanu. Koma ndinena Ine coonadi ndi inu; kuyenera kwa inu kuti ndicoke Ine; pakuti ngati sindicoka, Nkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita ndidzamtuma Iye kwa inu. Ndipo atadza Iyeyu, adzatsutsa dziko lapansi za macimo, ndi za cilungamo, ndi za ciweruziro; za macimo, cifukwa sakhulupirira Ine; za cilungamo, cifukwa ndinka kwa Atate, ndipo simundionanso; za ciweruziro, cifukwa mkuru wa dziko iri lapansi waweruzidwa.” 
 

Kodi ntchito za Mzimu Woyera ndi chiani?
Amatsutsa dziko la uchimo, la chilungamo, ndi la chiweruzo.

Mu Genesis 1:2 munalembedwa kuti, “Dziko lapansi ndipo linali lopanda kanthu; ndipo mdima unali pamwamba pa Nyanja; ndipo mzimu wa Mulungu unalinkufungatira pamwamba pa madzi.” Tingaone kuchokera mu ndimeyi kuti Mzimu Woyera sumakhala mu mitima yodzala ndi chisokonezo komanso uchimo, koma umakhala m’mitima yokha ya iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma. Komabe, anthu ambiri mu chisokonezo ndi kupanda kanthu kwao amagwa pansi pa zikhulupiliro zotentheka, ponena kuti akufuna kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera pamene ali ndi uchimo m’mitima yawo. 
Mzimu umene unalandiridwa kudzera mu chisangalalo chotentheka si Mzimu okoma. Ntchito ya Satana ili pa okhulupilira akusayeruzika otentheka, ndipo anthu otentheka amagwa mosabvuta mothandizidwa ndi chinyengo chake komanso mphamvu. Koma Mzimu Woyera ndi Mulungu Munthu amene ali wanzeru, waluntha ndipo ali ndi chifuniro choonadi. Iye anagwira ntchito pamodzi ndi Mulungu Atate komanso Mwana Wake Yesu Kristu popanga dziko lapansi. Tsopano tizaphunzira ntchito zimene Mzimu Woyera wachita m’dziko lino. 
 
 

Mzimu Woyera umatsutsa dziko la uchimo 


Kodi ntchito yoyamba imene Mzimu Woyera umachita ndi yotani? Iye amatsutsa dziko lauchimo. Anthu amene amatsutsidwa ndi Iye ndi iwo amene savomera uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi Yohane ndiponso mwazi wa pa Mtanda. Iye amatsutsa ochimwa onse ndi machimo a iwo amene sakhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. . 
 
 

Amatsutsa dziko la chilungamo cha Mulungu 


Kodi chinthu chachiwiri chimene Mzimu Woyera umachita ndi chiani? Umachitira umboni ku chilungmao cha Mulungu ndi chikwaniritso cha Yesu populumutsa ochimwa ku machimo awo. Yohane 16;10 akunena kuti, “Za cilungamo, cifukwa ndinka kwa Atate, ndipo simundionanso.” Tiyenera kudziwa kuti chilungamo cha Mulungu mu Baibulo chikutanthauza chiani. Chikutanthauza choonadi kuti Yesu anachotsa machimo onse a dziko lapansi kudzera mu ubatizo Wake ndi Yohane ndiponso kuti aliyense amene adzakhulupilira mwa Iye angakhale olungama kudzera mu chisomo cha Mulungu. Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi ndipo anavomera machimo onse a dziko lapansi, anakhetsa mwazi Wake pa Mtanda, ndipo anaukitsidwa ndi kukhala Mpulumutsi wa ochimwa onse. Uwu ndi uthenga wabwino okoma umene Mulungu anatipatsa ife. Yesu anachotsa machimo onse a dziko lapansi kudzera m’madzi ndi mwazi mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndipo anakhala Mbuye wa miyoyo yathu. 
Mzimu Woyera umathandiza anthu kuti akhulupilire mu uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi Yohane ndiponso mwazi Wake wa pa Mtanda, motero kuwathandiza iwo kupeza chikhululukiro cha machimo awo. Muyenera kudziwa kuti ntchito za Mulungu mu utatu ndi yogwirizana. Mzimu Woyera umagwira ntchito ya uthenga wabwino okoma, kupanga anthu kukhulupilira mu chikondi cha Mulungu. Iye amapangitsanso uthenga wabwino okoma oona wa madzi ndi Mzimu kukhala oona. 
 
 

Iye amatsutsa dziko lachiweruzo 


Kodi ntchito yachitatu ya Mzimu Woyera ndi chiani? Iye amaononga ntchito za Satana. Satana amanong’oneza m’maganizo mwa anthu, kunena kuti, “Mungakhulupilire mwa Yesu, koma ganizirani Chikristu ngati chimodzi cha zipembezo zambiri za padziko lapansi.” Satana amayesa kuletsa anthu kuti asakhulupilire mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda kuti asapeze chikhululukiro cha machimo awo ngakhale kuti amakhulupilira mwa Yesu. Chifukwa chakuti Satana amachepetsa Chikristu kukhala chipembezo “wamba” anthu ambiri amakhuzidwa ku chinyengo cha Satana kuti chifukwa chokhulupilira mwa Yesu ndi kukhala anthu abwino. Komabe, cholinga chenicheni cha kukhulupilira mwa Yesu ndi kukhala obadwa mwatsopano ngati anthu olungama. .
Simuyenera kukhala ndi chikhulupiliro chabodza. Chikhulupiliro chabodza sichingakupangitseni kukhala oyeretsedwa ngakhale mungakhulupilire mwa Yesu motani. Ngati muli ndi chikhulupiliro chabodza, simudzadziwa kapena kuona Yesu bwinobwino chifukwa cha mabodza a Satana. Mzimu Woyera umakhala lonjezo la chipulumutso kwa iwo amene anapulumutsidwa pokhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. Zikhulupiliro zonse za iwo amene ali ndi uchimo m’mitima yawo zilibe ntchito. 
Mzimu Woyera umanenera choonadi cha uthenga wabwino okoma. Yesu anabatizidwa kuti achotse machimo onse a dziko ndipo anapachikidwa kuti alipire mphoto ya uchimo. Mzimu Woyera umanenera ku choonadi chimenechi. Mzimu Woyera umachenjeza anthu onse a padziko lapansi kuti akhululukidwe ku machimo awo onse pokhulupilira mu uthenga wabwino oona. Komabe, tiyenera kusunga m’maganizo mwathu kuti Mzimu umatsutsa ndi kuweruza iwo amene satenga uthenga wabwino okoma m’mitima yawo. 
 

Aliyense ayenera kukhala ndi chikhulupiliro chodalitsika 

Kodi chikhulupiliro chodalitsika ndi chotani? Ndi chikhulupiliro chimene chimatitsogolera kukalandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera kudzera mu chikhululukiro cha uchimo. Komabe, tikuona Akristu ambiri padziko lonse lapansi amene akali ndi uchimo mu mitima yawo, ngakhale anasungabe chikhulupiliro chao mwa Yesu kwa nthawi yaitali. Pamene akhala nthawi yaitali akukhulupilira mwa Yesu, ndi pamene amakhalanso ochimwa kwambiri. Vuto lalikulu limene likuwatsekereza iwo kuti awomboledwe ku machimo awo ndi lakuti amaganiza kuti kulankhula m’malilime ndiponso kuona masomphenya ndi chizindikiro chakuti analandira Mzimu Woyera. Iwo sadziwa za chiweruzo cha Mulungu ku machimo awo. 
Anthu ambiri m’dziko lino sangasiyanitse ntchito za Mzimu Woyera ndi ntchito za Satana. Nchito za Satana zimatsogolera anthu muchisokonezo powapatsa iwo zikhulupiliro zabodza ndipo kenako kuwatsogolera iwo kuchionongeko. Ichi ndi chimene Satana amafuna kukwaniritsa mwa kuukira Mulungu. Satana amapangitsa anthu kuti akhale ndi chikhulupiliro cha malodza ndi kuwatenga iwo ngati akapolo ake. Satana amaika mwa iwo khumbo kuti aone zozizwitsa zauzimu ndi zodabwitsa powapangitsa iwo kuganiza kuti zochitika zotere ndiye zoyenera osati kulandira Mzimu Woyera kukhala mwa ife kudzera mwa kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma. 
Komabe, Mzimu Woyera umalola anthu kuona dziko la Mulungu kudzera m’Mawu. Kudzera mwa Mzimu Woyera, iwo anadziwa ndi kukhulupilira kuti Mulungu analenga munthu, ndiponso kuti Mulungu amawakonda iwo, ndipo kuti Mulungu akufuna kuwapulumutsa iwo. Chikonzero Chake kwa ochimwa chinali chakuti Yesu Kristu awapulumutse ku machimo awo kudzera mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndi kuwaitana kuti akhale Naye mu chikondi Chake mwa chikhulupiliro. 
1 Petro 3:21 akunena kuti, “Cimenenso cifuniro cace cikupulumutsani tsopano, ndicoubatizo.” Ndiponso, 1 Petro 1:23 akunena kuti, “Inu amene mudabadwanso, osati ndi mbeu yofeka, komatu yosaola, mwa mau a Mulungu amoyo ndi okhalitsa.”
Ntchito ya Mzimu Woyera ndi kuunikira munthu pa choonadi cha uchimo, chachilungamo, ndi cha chiweruzo, ndi kuwapanga iwo kuti akhulupilire zoonadi zimenezo. Mzimu Woyera umawapangitsa iwo kudziwa za chiweruzo cha Mulungu ndiponso kuti angaomboledwe ku machimo awo pokhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda. Mzimu Woyera umawapatsa iwo nzeru zakuti Iye ali mwa iwo pamene ali ndi chikhulupiliro mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. 
Kufika pano taona pa ntchito za Mzimu Woyera. Anthu onse a m’dziko lapansi angakhale ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera ndi chikondi cha Mulungu pokhapo ngati apeza chikhululukiro cha machimo pokhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. 
 

Khalidwe la Mzimu Woyera 

Mzimu Woyera ndi Mulungu Wamphamvu zonse. Iye ali ndi makhalidwe ofunikira aumunthu, otchedwa, luntha, kukhudzidwa, ndi chifuniro. Chifukwa chakuti Mzimu Woyera uli ndi luntha, Iye amafufuza ngakhale zinthu zamkati kwambiri za Mulungu (1 Akorinto 2:10) ndi mitima ya anthu. 
Chifukwa chakuti Mzimu Woyera uli ndi kukhudzidwa, Iye ndi amakondwa ndi iwo amene akhulupilira m’mawu a Mulungu, koma umabuula kwambiri ndi osakhulupilira. Ndiponso, olungama angamvere chikondi cha Mulungu kudzera mwa Mzimu Woyera. 
Mzimu Woyera umatchedwanso “mtonthozi.” Ichi chikutanthauza kuti Mzimu Woyera umathandiza olungama muzovuta, ndi kubweretsa chipambano kwa iwo, kumenyana ndi adani awo. Iye ali ndi luntha, kukhudzidwa, ndiponso chifuniro monga ife anthu timachitira, ndipo amakhala mwa iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. 
 

Ntchito ya Mzimu Woyera ndi yotere 

Mzimu Woyera umalola anthu kuzindikira choonadi cha chikhululukiro cha uchimo ndi kukhala m’mitima ya okhulupirira. Nchito yake ndi kuchitira umboni ku choonadi choti Yesu anachotsa machimo onse amtundu wa anthu kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi Wake (1 Yohane 5:6-8). Iye amatsitsimulanso akapolo Ake ndi oyera mtima mu mavuto alionse ndi kuwalimbikitsa kuti ayimenso. Iye Yekha amawapembedzera pamene sakudziwa chimene ayenera kupemphera (Aroma 8:26). Ndipo amapereka mpumulo kwa olungama mu mpingo wa Mulungu ndi kuwatsogolera iwo ku mawu Ake ochuruka (Masalmo 23).
 

Nchito za Mzimu Woyera mogwirizana ndi Baibulo 

Mzimu Woyera umatsogolera olungama kuti azindikire ndi kukhulupilira mu choonadi m’mitima yawo ndi kulalikira kwa ena. “Lemba liri lonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa ciphunzitso, citsutsano, cikonzero, cilangizo ca m’cilungamo” (2 Timoteyo 3:16).
“Funani inu m’buku la Yehova, nimuwerenge; palibe umodzi wa iye udzasowa, palibe umodzi udzasowa unzace; pakuti pakamwa pa Yehova panena, ndipo Mzimu wace wasonkhanitsa iwo” (Yesaya 34:16).
“Ndi kudziwa ici poyamba, kuti palibe cinenero ca limbo citanthauzidwa pa cokha, pakuti kale lonse cinenero sicinadza ndi cifuniro ca munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa Mzimu Woyera, analankhula” (2 Petro 1:20-21).
Mzimu Woyera unagwira akapolo a Mulungu kuti alembe mawu a Mulungu kuti ife tiwerenge. Anapereka kwa anthu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndi kutsogolera ife kuti tilalikire ku dziko lapansi. Motero, ngakhale kuti olungama angavutike ndi mayeso ambiri pa moyo wawo, amatha kuwagonjetsa zikomo pa mphamvu ya Mzimu Woyera. 
 

Mphatso ndi chipatso cha Mzimu Woyera 

Mphatso za Mzimu Woyera zikutanthauza maluso omwe amapereka kwa oyera mtima kuti afalitse uthenga wabwino okoma wa Mulungu kwa ena. Oyera mtima motero amazipereka okha ku ntchito ya Mulungu ndi mphatso imene anawapatsa, ndipo Mzimu Woyera umawathandiza iwo kuti apereke ulemelero kwa Ambuye. “Koma kwa yense kwapatsidwa maonekedwe a Mzimu kuti apindule nao” (1 Akorinto 12:7).
Cholinga cha mphatso ya Mzimu Woyera chinali kupatsa oyera mtima chikhulupiliro ndi kuwathandiza iwo kuthamanga mpikisano umene unali kutsogolo kwawo (Aefeso 4:11-12). Mzimu Woyera umapereka mphamvu kwa akapolo a Mulungu kuti uwathandize kufalitsa uthenga wabwino. Mpingo wa Mulungu ndi dera la oyera mtima amene ayeretsedwa mwa Yesu Kristu. (1 Akorinto 1:2). 
Mkristu aliyense amene analandira Mzimu Woyera ayenera kukhala mogwirizana ndi udindo wake ndi nchito, popeza Yesu Kristu ndi mutu wa mpingo. Mzimu Woyera umapereka kuzindikira kwa uzimu ndi mphamvu kwa oyera mtima kuti agwire nchito ya Ufumu wa Mulungu. Amachita zonse kuti aonetse ulemelero wa uthenga wabwino umene Mulungu anatipatsa ife. Iye anati, “Cifukwa cace mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale mucita kanthu kena, citani zonse ku ulemerero wa Mulungu” (1 Akorinto 10:31).
 

Mphatso zosiyanasiyana za Mzimu 

Pali mitundu khumi ndi iwiri ya mphatso ya Mzimu Woyera. Tingaone mu Baibulo kuti mphatso zimenezi zimaoneka m’kaonekedwe osiyanasiyana kwa anthu osiyanasiyana. M’ndandanda wa mphatso zimenezi waoneka mu Aroma 12:6-8, 1 Akorinto 12:8-10, ndiponso Aefeso 4:11. Zotsatirazi ndi mphatso zisanu ndi zinai za Mzimu zimene zinanenedwa mu 1 Akorinto mutu 12.

1) Mawu a chidziwitso: Ichi chimatipatsa ife nzeru za kumvetsetsa uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu ndi kutilola kulalikira uthenga wabwino okoma. 
2) Mawu a nzeru: Izi ndi mphamvu za kukonza mavuto athu amene amabwera mu moyo mwa olungama kudzera mu mawu olembedwa a Mulungu. 
3) Chikhulupiliro: Mzimu Woyera umapereka chikhulupiliro cholimba ndi chilimbikitso kwa oyera mtima kuti achite chodabwitsa chopulumutsa miyoyo ku machimo awo ndiponso Satana. Munthu olungama angakhululukidwe machimo ndi kuchiritsa mavuto auzimu kudzera mu mphamvu ya chikhulupiliro. 
4) Machiritso: Mzimu Woyera umapereka mphamvu ya kuchiritsa anthu olungama kudzera mu chikhulupiliro chawo mu mawu a Mulungu. 
5) Machitidwe a mphamvu: Iyi ndi mphatso yodzidzimutsa imene imalola oyera mtima kuchita ntchito ya Mulungu pokhulupilira m’mawu a Mulungu. Chozizwitsa ndi chinthu chimene chimachitika mwauzimu kudzera m’chikhulupiliro, kupitilira pa nzeru za munthu za lamulo la dziko. 
6) Chinenero: Pa nthawi imeneyi, okhawo amene akhulupilira ndi kumvera mawu a Mulungu ndi amene angachite uneneri mogwirizana ndi zimene zinalembedwa. Mawu a munthu wina amene ali ndi zikhulupiliro zomwe sizikuchokera ku zimene zinalembedwa mu Baibulo sangakhale mneneri oona. Akapolo a Mulungu, amene ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera, amalalikira mawu a Mulungu ndipo motero amawalimbikitsa ndi kuwakakamiza iwo kuti achite ntchito Yake kudzera mu mpingo, umene ndi thupi la Mulungu. Mzimu Woyera unapereka mphamvu imeneyi kwa akapolo a Mulungu ndi oyera mtima. 
7) Chizindikiro cha mizimu: Iyi ndi mphamvu ya kudziwa ngati machimo a wina wake akhululukidwa. Ndi zotheka kwa ife kusocheretsedwa ndi Satana ngati tiribe mphatso imeneyi. Chifukwa dziko lino liri pansi pa ulamuliro wa Satana, tingakhale ndi mphatso imeneyi mwa kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma umene Mulungu anapereka kwa ife ndipo motero kugonjetse mayeso, zolemetsa ndi zoipa m’dziko lino. Munthu olungama amalandira mphatso imeneyi pokhulupilira mu uthenga wabwino oona. Iye motero angathe kunena ngati munthu ali ndi uchimo mu mtima mwake. 
8) Kulankhula malilime a mitundu mitundu: Baibulo limatiuza ife za kulankhula m’malilime: “Ndifuna kulankhula mau asanu ndi cidziwitso canga, kutinso ndikalangize ena, koposa kulankhula mau zikwi m’lilime” (1 Akorinto 14:19). Oyera mtima ayenera kudziwa kuti ndi kofunikira kwambiri kumvetsetsa mawu a Mulungu a choonadi m’malo momalankhula m’malilime m’mene iye yekha satha kumvetsetsa. Iye motero ayenera kupewa kulankhula m’malilime. 
9) Kumasulira malilime: Mphatso imeneyi inaperekedwa kwa ophunzira kuwalola iwo kuti alalikire uthenga wabwino m’nthawi ya mpingo oyambilira. Masiku ano Mzimu Woyera umafalitsa uthenga wabwino kudzera mu utumiki wa kumasulira ndi kutanthauzira uthenga wabwino m’zilankhulo zosiyanasiyana. Sipafunika omasulira ngati munthu amene akulalikira uthenga wabwino angakwanitse kulankhula zilankhulo zina. Komabe, pamene takumana ndi vuto la chilankhulo, Mulungu nthawi zonse amatilola ife otanthauzira kuti tikwaniritse ntchito Yake. Mulungu samagwira ntchito mosokoneza kapena mwachisangalalo. Mzimu Woyera umagwira ntchito mu uthenga wabwino okoma ndipo umatsogoleranso oyera mtima kuti amasulire uthenga wabwino mu zilankhulo zosiyanasiyana 
 

Kodi zipatso za Mzimu Woyera ndi zotani? 

Poganizira za zipatso za Mzimu Woyera, Baibulo limatiuza kuti, “Koma cipatso ca Mzimu ndico cikondi, cimwemwe, mtendere, kuleza mtima, cifundo, kukoma mtima, cikhulupiriro, cifatso, ciletso; pokana zimenezi palibe cilamulo” (Agalatiya 5:22-23).

1) Chikondi: Chikondi choona ndi cha olungama kuti apulumutse ochimwa onse kumachimo awo mwa kulalikira uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. Chifukwa anthu olungama ali ndi uthenga wabwino okoma umene ndi chikondi choona cha Yesu, amalalikira uthenga wabwino wa chikondi choona ku miyoyo ya ena. 
2) Chimwemwe: Uwu ndi ulemelero wachisangalalo chosaneneka ochokera pansi pa mitima yathu pamene takhala obadwa mwatsopano. Munthu olungama amene wakhululukidwa machimo ake ali ndi chimwemwe mu mtima mwake (Afilipi 4:4). Chifukwa muli chimwemwe m’mitima ya olungama, ali ndi mphamvu ya kugawa chimwemwe chawo ndi ena. 
3) Mtendere: Uwu ndi mtima wotsitsimula umene umaperekedwa kwa munthu olungama amene anakhululukidwa machimo ake pokhala ndi chikhulupiliro mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu. Mzimu Woyera umapangitsa olungama kulalikira uthenga wabwino okoma wamtendere. Anthu amene anamva uthenga wabwino okoma wamtendere umenewu amatsogolera ena kuti agonjetse machimo a dziko ndiponso kukhala ndi nzeru za mphamvu za chikhulupiliro ndi chilimbikitso mu mphatso ya chipulumutso. Anthu olungama amene amapanga mtendere pakati pa Mulungu ndi mtundu wa anthu akutchedwa ana a Mulungu (Mateyu 5:9) ndi kutsogolera ena kuti alandire chikhululukiro cha uchimo (Miyambo 12:20). Mzimu Woyera umapangitsa olungama kukhala ndi miyoyo yolungama ndi kudalitsa ena ndi mtendere pofalitsa uthenga wabwino okoma. 
4) Kuleza Mtima: Zipatso za kuleza mtima zili mu mtima mwa olungama, amene anaomboledwa ku machimo awo pokhulupilira mu uthenga wabwino okoma. Tingakhale ndi chipatso chotere pokhala ndi nzeru zochuruka za chiyanjano ndi Mzimu Woyera. Muli mtima wa kuleza mtima ndiponso chipiliro mwa olungama. 
5) Chifundo: Mulungu anali ndi chifundo pa ife pamene tinali odzala ndi uchimo ndipo anatiombola ku machimo athu onse kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda. Tingakonde ndi kukhala ndi chifundo ndi ena chifukwa Yesu anali ndi chifundo pa ife ndipo anachotsa machimo athu onse, ndipo chifukwa tinakhulupilira mwa Iye ndi kulandira chisomo Chake. Olungama ali ndi mitima yodzala ndi kukoma mtima ndi zipatso za uthenga wabwino okoma. 
6) Kukoma mtima: kukoma mtima apa kukutanthauza “ubwino.” Anthu olungama ali ndi ubwino ndiponso chikhulupiliro mwa Ambuye pansi pa mitima yawo. 
7) Chikhulupiliro: Chikhulupiliro chikutanthauza mtima odzala ndi chikhulupiliro mwa Mulungu. Chikhulupiliro mwa oyera mtima chichokera mwa kuzichepetsa kwa Yesu. 
8) Chifatso: Ichi chikutanthauza kukhala ndi mphamvu yodzala ndi kumvetsetsa ena ndi kuwagwira mowatenthetsa ndiponso mwachikondi mu mtima mwathu. Olungama ali ndi mitima ya kukonda adani awo ndi kupempherera chiombolo chawo. 
9) Chifatso: chifatso ndi mphamvu ya kuziona wekha, kupewa kukhala moyo osayenera ndipo m’malo mwake kukhala wekha odziletsa. 
 

Kukhala odzadzidwa ndi Mzimu Woyera 

Kodi zoturuka zake ndi zotani zodzadzidwa Mzimu Woyera? Kulandira madalitso awa ndi kulola oyera mtima kukhala ngati ophunzira a Yesu Kristu, kuzilumikiza okha ku mpingo wa Mulungu. Mzimu Woyera umapangitsa olungama kukhala ziwiya za chilungamo ndi kuzipereka okha kuti akwaniritse chifuniro cha Kristu. Chifuniro cha olungama chimalamuliridwa ndi chifuniro cha Ambuye, ndipo mwakufuna kwawo amapereka katundu wawo ndi matalente kwa Iye. Mzimu Woyera umapangitsa olungama kukhala moyo odzipereka kuti agonjetse machimo a dziko ndi nzeru ya chigonjetso, chimwemwe ndi chilimbikitso, osati umphawi wakuuzimu kugonja kapena kukwiya (Aroma mutu 7).
“Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ace a dziko” (Machitidwe 1:8). Kudzadzidwa kwa Mzimu Woyera kumatsogolera olungama kulalikira uthenga wabwino. 
Ambuye anapereka nzeru yamphamvu ya chikhulupiliro kwa iwo amene Mzimu Woyera ukhala mwa iwo. Ndipo Mulungu anapereka ufulu okhala ana Ake kwa iwo amene machimo awo anakhululukidwa pokhulupilira kwawo uthenga wabwino okoma wa Yesu (Yohane 1:12). Anthu olungama amene akhala ana a Mulungu kudzera m’chikhulupiliro angalalikire uthenga wabwino okoma m’dziko lino. 
Anthu olungama ali ndi mphamvu yogonjetsa Satana kudzera mu uthenga wabwino wa chikhululukiro cha machimo. Iwo alinso ndi mphamvu yakuchiritsa matenda auzimu(Marko 16:18), kupondereza pa mphamvu za Satana (Luka 10:19), ndi kulowa mu Ufumu wa Kumwamba (Chivumbulutso 22:14). Anthu olungama amakhala ndi ulamuliro umodzi monga mafumu pokhulupilira m’mawu a Mulungu a lonjezo (2 Akorinto 6:17-18).
Mzimu Woyera umapangitsa anthu olungama kuti ataye zilakolako zonse za dziko. Iye amatitsogoleranso kuti tilalikire uthenga wabwino oona (Agalatiya 5:6).
Mzimu Woyera umapangitsa olungama kuti awerenge ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma ndiponso kuphunzitsa uwo kwa ena (1 Timoteyo 4:13).
Mzimu Woyera umasonkhanitsa olungama ku mpingo wa Mulungu masiku onse (Ahebri 10:25). 
Mzimu Woyera umapangitsa olungama kubvomereza machimo awo. (1 Yohane 1:9) kuti apange mitima yawo kutsutsidwa ndi choonadi (Aefeso 5:13).
Mzimu Woyera umatsogolera olungama ku njira yoyenera mu miyoyo yawo. (Masalmo 23).
Mzimu Woyera umauza olungama kuti asazimitse mphatso Zake (1 Atesalonika 5:19).
Mzimu Woyera umachita ntchito zazikuru kudzera mu uthenga wabwino wodabwitsa (Marko 16:17-18).
Mzimu Woyera umatsogolera olungama kukhala ngati ophunzira a Ambuye mwa kulumikizana nawo mu mpingo wa Mulungu. Amatsogolera olungama kuti akhale ndi miyoyo yauzimu ya kulalikira uthenga wabwino okoma ndi kudzadzidwa ndi Mzimu Woyera. Iyi ndi ntchito ya Mzimu Woyera kudzera mu uthenga wabwino wodabwitsa (1 Petro 2:9).
Iye akugwira ntchito m’mitima ya oyera mtima pa nthawi ino. Aleluya!