• All e-books and audiobooks on The New Life Mission website are free
  • Explore multilingual sermons in global languages
  • Two new revised editions in English have been released
  • Check out our website translated into 27 languages
Search

Sermons

Mutu 8: Mzimu woyera

[8-14] Kodi Kulapa Koona Kumene Kumatitsogolera Ife Kuti Tilandire Mzimu Woyera ndi Kotani? (Macitidwe a Atumwi 2:38)

Kodi Kulapa Koona Kumene Kumatitsogolera Ife Kuti Tilandire Mzimu Woyera ndi Kotani?(Macitidwe a Atumwi 2:38)
“Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m’dzina la Yesu Kristu kuloza ku cikhululukiro ca macimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.”
 

Kodi kulapa koona komwe kukufunika kuti tilandire Mzimu Woyera ndi kotani?
Ndi kubwerera ku uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu ndi kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda.

Baibulo limanena mu Machitidwe a Atumwi 2 kuti ulaliki wa Petro unatsitsimula anthu kwambiri ndipo unapangitsa kuti alape ku machimo awo. Anavutika kwambiri mu mtima mwawo ndipo anati kwa Petro ndi atumwi onse, “Tidzacita ciani amuna, abale?” (macitidwe a Atumwi 2:37) Kenako Petro anayankha kuti, “Lapani, batizidwani yense wa inu m’dzina la Yesu Kristu kuloza ku cikhululukiro ca macimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera” (Macitidwe a Atumwi 2:38). 
Ulaliki wa Petro ukuonetsa poyera kuti chikhulupiliro mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu ndi koyenerera kuti tilandire Mzimu Woyera ndipo ukutionetsanso kuti kulapa koona ndi chiani. Tiyenera kudziwa kuti tingalandire Mzimu Woyera pamodzi ndi chikhululukiro cha machimo poyang’ana kwambiri pa Malemba ndi kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. 
Chinthu choyamba chimene tiyenera kukhala nacho kuti tilandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera ndi chikhulupiliro mwa kulapa kwa m’baibulo. Komabe, tiyenera kukhala ochenjera kuti tisatanthauze kulapa kumeneku ngati chisoni. Kulapa apa kukutanthauza chikhulupiliro mwa Yesu Kristu. Tingathe kuona mu Baibulo kuti anthu anamva kale chisoni atapachika Ambuye. Anamva chisoni kupempha Petro kuti achite chiani ndipo anabvomereza machimo awo ngakhale kwa Petro asanawauze kuti alape. Tingathe kuona mwa ichi kuti kulapa kumene Petro anali kunena sikunali kwakumvera chisoni uchimo kapena kuulula, koma kutenga Yesu Kristu mu mtima mwa munthu ngati Mpulumutsi wake ndi kukhala ndi chikhulupiliro mu uthenga wabwino okoma umene Iye anatipatsa ife. Ichi ndi chilengedwe choona cha kulapa. 
Chikondi cha Yesu Kristu chinabwera kwa ife padakalibe chisoni-chamunthu cha machimo a m’mitima yathu. Ichi chikutanthauza kuti Yesu anachotsa machimo athu pamene anabatizidwa mu Mtsinje wa Yordano, kufa pa Mtanda ndi kuukanso kwa akufa. Mwa njira imeneyi, anayeretsa ku machimo ndi mphulupulu zathu onse. 
Kulapa koona kukutanthauza kukhulupilira mu choonadi chimenechi. Kodi muganiza kuti machimo athu adzachoka kosatha, ngati tangomvera chisoni machimo athu ndi kupempha chikhululukiro? Uku sikulapa koona. Kulapa koona kukutanthauza kulandira chikhululukiro cha machimo athu pokhulupilira mu uthenga wabwino okoma wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake. Baibulo limanena kuti tiyenera kukhululukidwa machimo athu mwa kulapa. Chimodzimodzi, tiyenera kukhulupilira mu uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake kuti tilandire chikhululukiro chonse cha machimo athu. 
Petro anapereka ubatizo “m’dzina la Yesu Kristu” kwa iwo amene anakhulupilira mwa Yesu. Yesu anabatizidwa kuti achotse machimo a mtundu wa anthu. Ubatizo wake ndi imfa yake pa Mtanda inali kumaliza Kwake kwa uthenga wabwino okoma umene unapangitsa okhulupirika kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera (Mateyu 3:15-17). Mtundu wa anthu ungayeretsedwe pokhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda. Mwachidule, iwo amene analandira chikhululukiro cha machimo pokhulupilira mu uthenga wabwino alandira Mzimu Woyera. 
 
 

Kodi pemphero lingabweretse kukhazikika kwa Mzimu Woyera?


Anthu sangalandire chikhululukiro cha machimo ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera ngakhale angapemphere molimba bwanji kuti aulandire. Kuti tikhale ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera, ndikofunikira kukhulupilira mu uthenga wabwino okoma umene unakwaniritsidwa ndi ubatizo wa Yesu ndiponso mwazi Wake pa Mtanda. Mzimu Woyera wa Mulungu umapatsidwa kwa iwo okha amene machimo awo anatsukidwa kwathunthu. 
Chikhulupiliro mu uthenga wabwino chikutanthauza kudziwa Yesu Kristu ngati Mpulumutsi oona. Macitidwe a Atumwi 2:38 amanena kuti, “Lapani, batizidwani yense wa inu m’dzina la Yesu Kristu kuloza ku cikhululukiro ca macimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.” Mtumwi Petro ananena kuti kukhazikika kwa Mzimu Woyera kumaperekedwa kwa iwo amene akhululukidwa machimo awo kudzera mu chikhulupiliro cha kulapa koyenera. Chikhululukiro cha machimo ndi kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera ndi zogwirizana. 
Baibulo linena kuti, “Lapani, batizidwani yense wa inu m’dzina la Yesu Kristu kuloza ku cikhululukiro ca macimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. Pakuti lonjezano liri kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana” (Macitidwe a Atumwi 2:38-39).
Munthu angalandire Mzimu Woyera pachifukwa chokha chakuti mtima wake wayeretsedwa ndipo ulibe uchimo. Motero, tiyenera kukhulupilira mu uthenga wabwino umene Yesu Kristu anapereka kwa ife. Tiyenera kukhala oyeretsedwa titapeza chikhululukiro cha machimo athu pokhulupilira mu uthenga wabwino umene umanena kuti machimo onse a dziko anatsukidwa pamene Yesu Kristu anabatizidwa. Pokhapo ndi pamene tingalandire Mzimu Woyera. Ndi chifuniro cha Mulungu kuti Mzimu Woyera ukhale mwa anthu. “Pakuti ici ndi cifuniro ca Mulungu, ciyeretso canu” (1 Atesalonika 4:3). 
Chikhululukiro choona sichipatsidwa kudzera mu mphamvu za anthu, nsembe kapena kuchita zabwino, koma pokhulupilira kokha mu uthenga wabwino okoma umene Mulungu, Mtatu Woyera anatsiriza kudzera mwa Yohane Mbatizi. Mulungu, Mtatu Woyera, anapereka kukhazikika kwa Mzimu Woyera kwa iwo amene anakhululukidwa pokhulupilira mu uthenga wabwino okoma. 
Khamu la anthu linalasiwa mu mtima pamene linamvera zimene Petro ananena pa Tsiku la Pentekoste Anafuula mokweza, “Tidzacita ciani amuna, abale?” (Machitidwe a Atumwi 2:37) Ichi chikuonetsa kuti anasintha maganizo awo ndipo tsopano anakhulupilira mwa Yesu ngati Mpulumutsi wawo. Anapulumutsidwanso ku machimo pokhulupilira mu kulapa koona kumene Petro analalikira. Kukhululukidwa kwa machimo kunapatsidwa kwa anthu onse malingana ndi chikhulupiliro chawo mu Uthenga wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda.
Cholinga cha ubatizo wa Yesu chinali chomulola iye kuti anyamule machimo a dziko. Chikhulupiliro mu chimenechi ndi chinthu chofunikira kwambiri kuti mulandire Mzimu Woyera. Mulungu amapereka kukhazikika kwa Mzimu Woyera kwa iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino wa choonadi wochokera mu ubatizo wa Yesu. “Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anaturuka m’madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutero pa Iye” (Mateyu 3:16). Kubwera kwa Mzimu Woyera pa Tsiku la Pentekoste uli ndi ubale wapadera ndi chikhulupiliro cha atumwi mu uthenga wabwino okoma: ubatizo wa Yesu, imfa Yake pa Mtanda ndi kuukanso Kwake. 
Machitidwe a Atumwi akunena kuti anthu anabatizidwa m’dzina la Yesu ndipo analandira Mzimu Woyera. Tiyenera kukhulupilira kuti kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera ndi mphatso ya mtengo wapatali yochokera kwa Mulungu. Kuti tilandire mphatso ya Mzimu Woyera, machimo athu onse ayenera kutsukidwa kudzera mu chikhulupiliro mu ubatizo wa Yesu ndi imfa Yake ya pa Mtanda.
Mogwirizana ndi Machitidwe a Atumwi, onse amene anamvera uthenga wabwino wa Petro, m’mene ananena kuti, “Mudzipulumutse kwa mbadwo uno wokhotakhota” (Macitidwe a Atumwi 2:40), anamvera langizo lake ndipo anabatizidwa. Chimene tikuphunzirapo kuchokera mu Baibulo ndi chakuti atumwi m’masiku a mpingo oyambirira analandira Mzimu Woyera chifukwa cha chikhulupiliro chawo mu ubatizo wa Yesu Kristu ndi mwazi Wake pa Mtanda. Ichi ndi chinthu chofunikira kwambiri kuti mulandire Mzimu Woyera. Kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda ndi kofunika kwambiri ngati munthu akufunafuna chikhululukiro cha uchimo. 
 
 

Chikhulupiliro chimene chimatitsogolera kuti tilandire Mzimu Woyera kudzera mu kulapa koona


Tiyeni tione mu Macitidwe a Atumwi 3:19. “Cifukwa cace lapani, bwererani kuti afafanizidwe macimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zacokera ku nkhope ya Ambuye.” Kodi kulapa tingakufotokoze motani? Tiyeni tiganize za izi kachiwiri. 
Mu Baibulo, kulapa kukutanthauza kubwerera ku chikhululupiliro cha chiombolo. M’masiku amenewo, anthu anali kuchita ngati m’mene anali kufunira ndipo anali kupembeza zinthu zimene Mulungu analenga. Koma pamene anazindikira kuti Yesu Kristu anawapulumutsa ku machimo awo ndi madzi komanso mwazi, anasinthidwa. Uku ndi kulapa kwa m’baibulo. Kulapa koona ndi kubwerera ku uthenga wabwino okoma wa madzi ndi Mzimu. 
Kodi kulapa koona kukufunika chiani kuti tilandire Mzimu Woyera? Ndi kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda. “Nyengo zakutsitsimutsa zacokera ku nkhope ya Ambuye” Ngati anthu ali ndi chikhulupiliro chimenechi, amakhululukidwa ku machimo awo ndi kulandira Mzimu Woyera. Chifukwa Yesu anayeretsa ochimwa onse m’dziko kudzera mu ubatizo Wake ndi mwazi Wake wa pa Mtanda, tiyenera kukhulupilira mu Uthenga wabwino okoma unemewu, kupeza chiombolo ndi kulandira Mzimu Woyera. 
Kuti tikhulupilire mwa Yesu ndi kulandira kukhazikika kwa Mzimu Woyera, machimo a munthu ayenera kuperekedwa pa Yesu kudzera mwa kukhulupilira mu ubatizo Wake ndi imfa pa Mtanda. Tiyenera kukhulupilira kuti Yesu ananyamula machimo athu onse ndi kufa pa Mtanda kuti aweruzidwe chifukwa cha machimo athu. Ichi ndi chikhulupiliro choona ndi kulapa koona, kumene kumatilola ife kuti tikhale ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera. 
Mzimu Woyera umabwera kwa iwo amene ali chikhululukiro cha machimo awo. Kodi ndi chifukwa chiani Mulungu anapereka Mzimu Woyera ngati Mphatso kwa iwo amene ali ndi chiombolo? Chifukwa Mzimu Woyera, pokhala woyera, umafuna kukhala mkati mwa iwo ndi kuwasindikiza iwo ngati ana Ake. 
Mzimu Woyera ndi Mulungu. Atate, Mwana, ndi Mzimu Woyera ndi Mulungu m’modzi. Ndi anthu atatu, koma ndi Mulungu m’modzi kwa iwo amene amakhulupilira mwa Yesu. Atate anali ndi chikonzero chopulumutsa ife ku machimo athu ndipo Yesu Mwana anabwera padziko lino, anabatizidwa ndi Yohane kuti achotse machimo a dziko lapansi, anafa pa Mtanda, anaukanso kwa akufa pa tsiku lachitatu ndipo anatengedwa kupita kumwamba. Mzimu Woyera umatitsogolera kuti tikhulupilire mu uthenga wabwino okoma umenewu pochitira umboni za ubatizo wa Yesu ndi mwazi Wake wa pa Mtanda. 
Mulungu anasindikiza iwo amene anapulumutsidwa kudzera mwa Mzimu Woyera. Ambuye amapereka Mzimu Woyera kwa iwo amene amakhulupilira mu uthenga wabwino umene Yesu anachotsera machimo a dziko. Mulungu amawapatsa Mzimu Woyera ngati lonjezo powasindikiza iwo ngati ana Ake. Mzimu Woyera ndi chitsimikizo chomaliza wa chipulumutso cha uchimo kwa iwo amene akhulupilira mu uthenga wabwino okoma. 
Iwo amene ali ndi Mzimu Woyera ndi ana a Ambuye. Iwo amene ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera nthawi zonse amamva kutsitsimutsidwa. Ali ndi chikhulupiliro cholimba mu mawu a Mulungu, mu ubatizo wa Yesu ndiponso mu mwazi wa pa Mtanda. Iwo ndi okondwadi. Iwo amene amalapa m’njira yabwino alibe uchimo m’mitima yawo ndipo ali ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera. 
Baibulo limanena kuti kuli kulapa kumene kumabweretsa chikhululukiro cha machimo. Kodi munapitamo mu kulapa kotere? Ngati munalapa ndipo munapeza zikhulupiliro zoona, inunso mungalandire uthenga wabwino okoma. Ndikulangizani inu kuti mulape machimo anu ndi kulandira Mzimu Woyera. Kodi mwakonzeka kulapa ndi kukhulupilira uthenga wabwino okoma umene umatsogolera kuti mulandire kukhazikika kwa Mzimu Woyera?